Skip to main content

Full text of "KUR'AN----PRIJEVOD NA PREKO 40 JEZIKA"

See other formats




Translation of the Meanings of 

THE NOBLE QURAN 

in the Chichewa Language 



— „, 




&mm&\\mm 





Myang'aniri wa Mizikiti iwiri Yolemekezeka 

Mfumu Fahd Bin Abdul 'Aziz Al Saud, Mfumu ya 

Saudi Arabia ndi okondwa polamula kusindikiza 

Buku la Qur'an lotanthauzidwa 









,„ „->. , ,■„„ , . m"^;^;^;^^^ 




Nyumba ya Mfumu Fahd 
yosindikizira Qur'an yopatulika 



**~~~~~~ ~» „ , ..„.. ...,„ , ,_^ ., , ^ 



7*-y£j\ Jt X+^*J* /wi ^jyJ|JL*P V,J ?JL^ ye.j.>t-'l <Jb^ *-*£» 

^L-ijVlj 5j_pjJ!j cJUjVlj i-w.^L— y\ oj3_^JI yjj 

: ^1 <ol^ J J3UJI 4 o*iWI VJ & JuJ " 1 

: J3UJI 4 ju^ L~j t cA-^b *-W»^' ^->j-^f ^ fM-Jlj stA^JIj 

. «<uApj oljiJl (J~ j>« ^^» 

rjbuU 

4 aj^*-«JI a-jj-«JI a£LJlL ^LijVlj S^jJIj cJUjVlj i-^^^L- »Vl jjj-iJI Sjljj ^ Ulclj 

^JL.Al ^jip a^^jI ^>L^ j 4 4 4»$ll oL*AM ^-*-=r ^1 ' /O^' of^iM ^ L«^ ^-^>-y ^c-**^ 

. «4jI _jJj ^^p iyJL» : ||£ ^Jy ^ <j j^lil f!)LiJ U^j 4 A^yJl ^ ^j^Ul 
^jjjJLJI <Jbt-s*il ipUJ JL$J ciJULil *l*_£ k-.Jbj 4 l^-JLj-iJl oJL. j^iktJ! LjI^'V ^L«Jl>-j 
*-jA^I jjl>- ^jjl UJLfrf ^1 4 lj.JLJL3l <iL 4-aj^jJI oJL* r^l &jUJU ^JLL jf 4 5jyil ioJlL 

. Lojy JU^»t« ^-~*^ ^-iJlj 4 Vl-Ul ^*p Aiil-UP ^-JJl £-*Jrl JJ ^ I^a^-Ijj 4 NIij 

. ^Ul <J *uLj (jfj 4 £^3l <p-^ 

^yUil *.bf ^p 0j-vtf»l5 Oj^— » -Lfiw OviL L^j- £^^-Jl olyjJl ^ L»oo i^-jS of iij-xJ LjI 
L. iLva^ ^ Irl 4-^j-yJI l^.^ ^yJl ^iUil ofj 4 jj^t cyLr^ 1 <J^* WJ^ J-^i <>Jl A-^JajJt 
. ^^aij lla>- J^ 4K j-lJl J^P ^^Uj U l^ijiM <ifj 4 ^^1 4JAI ^jllS" ^3 ^ ^j^l pi* <iL 
i^Jjj-tJi t*_ipfcsdll ipUaJ Xp kiUil ^*J>t^ ^'^d «jf <*>-jZ}\ o-lgJ ^jl5 JS" ^ y>-J> Ji j^j 
^ oL^lj-J^—»Vi oJL* ^a o^Li^U 4 o^Lij jf ^^tfii jf Ua>- ^ \ g J o-L>tj JLi lr Aj^-jJI AJu jlLL 

. ajiif *.Li ol i»^UJl cj^AiJI 



Ill 

BISMILLAH RAHMAN RAHIM 

MAU OYAMBA 

Wolemba: Wolemekezeka Sheikh 
Saleh Bin Abdul Aziz Bin 
Muhammad Al al-sheikh, 
nduna ya zachisilamu, chuma 
chopelekedwa mnjira ya mulungu, 
dawah ndi kutsogolera ku njira 
yoongoka, ndiponso wankulu 
woyang'anira nyumba yosindikizira. 

Kutamandika konse ndi kwa Mulungu bwana wa 
zolengedwa zonse, amene adanena m'buku lake 
lolemekezeka kuti: "Kwakufikani inu kuchokera kwa 
mulungu kuwunika ndi buku lofotokoza chilichonse "ndipo 
chipulumutso ndi mtendere zikhale kwa olemekezeka wa 
aneneri ndi atumwi onse, mthenga wa mulungu 
Muhammad amene adanena kuti; " wabwino mwa inu ndi 
amene waphunzira Qur'an ndi kuiphunzitsa". 

Pambuyo pake: 

Pofuna kukwaniritsa malangizo a wotumikira wa malo 
awiri olemekezeka ndiponso oletsedwa mfumu Fahd 
Abdul Aziz Al Saudi,Mulungu amusunge chifukwa 
chakuliganizira buku la Mulungu, ndikugwira ntchito 
yolifewetsera njira yofalitsira, ndikuligawa kwa Asilamu 
onse kuyambira kum'mawa ndikumadzulo kwa dziko 
lonse, kulifotokozela ndi kulimasulira kwake mzinenero 
zosiyana-siyana mdziko lonse, ndiponso ndichikhulupiriro 
cha unduna wa zachisilamu, chuma chopelekedwa mnjira 
ya Mulungu, dawa ndi kutsogolera kunjira yoongoka 
m'ndziko la Saudi Arabia, mwakufunika kwa kumasulira 
matanthauzo a Qur'an yolemekezeka mzinenero zonse 
zofunika za dziko lonse, ndi cholinga choti Asilamu onse 
omwe chinenero chawo si chiarabu, ndikufunitsitsa 
kufalitsa komwe mtumiki adalamula kuti: "falitsani zaine 
ngakhale ndime imodzi yokha". 



IV 



Ndipo pofuna kuwathandiza abale anzathu omwe 
amalankhula chinenero cha Chichewa, a Nyumba 
yosindikiza buku lolemekezeka la Qur'an ya mfumu 
Fahd ku Madinah Munawwarah, ali osangalala 
kupeleka kwa wowerenga wolemekezeka tanthauzo la 
bukuli m'chichewa lomwe anamasulira Sheikh Khalid 
Ibrahim ndipo analiona kumbali ya nyumbayi Sheikh 
Abdallah Omar Issa Mdala mothandizana ndi Sheikh 
Shaib Muhammad Mzoma. 

Choncho tikuyamika Mulungu wapamwamba-mwamba 
povomereza kuti ife tithe kugwira ntchito yaikuluyi 
yomwe tikulaka-laka kuti ikhale mwachifuniro cha 
Mulungu yekhayo ndikutinso anthu athandizike nayo. 

Ife tikudziwa kuti ntchito yomasulira matanthauzo a 
Qur'an yolemekezeka, ngakhale ikongole chotani,singafanane 
ndi matanthauzo eni-eni a Qur'an ya m'charabu 
yozizwitsa, ndikutinso matanthauzo omwe akumveka 
mukumasuliraku ndi olingana ndi m'mene kuliri kuphunzira 
kwa omasulira wake polimva Buku lolemekezeka la 
Mulungu, ndikutinso monga munthu wina aliyense, 
ntchitoyi singakhale yopanda kulakwitsa ndi kupunguka, 

Choncho tikupempha kwa wowerenga wina aliyense 
amene angazindikire zolakwika, kupunguka kapena 
kuonjezera kuti aidziwitse nyumba yosindikizira buku la 
Qur'an ya mfumu Fahd yomwe ili ku Madinah 
Munawwarah. Izi zizakhala zothandiza posindikizanso 
bukuli mtsogolo Mulungu akafuna. 

Mulungu ndiye wothandiza ndiponso muwongoli kunjira 
yoongoka. Ambuye Mulungu tilandireni ife ndithudi inu 
ndinu wakumva wodziwa. 



V 



M'dzina la Mulungu Wachifundo chambiri Wachisoni 

MAWU A OTANTHAUZIRA QUR'AN 

Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa. 
Madalitso ndi mtendere zikhale pa Mtumiki Muhammadi (S.A.W), 
akubanja lake ndi onse omutsatila. 

Qur'an ndi mawu a Mulungu amene adavumbulutsidwa kwa 
Mtumiki Muhammad (S.A.W), omwe sadasinthidwe chiganizo kapena 
lemba lirilonse ngakhale pang'ono ndipo idzasungidwa chomwecho 
mpaka tsiku la Chimaliziro.Mulungu wapamwamba walichita buku 
lakeli kuti likhale uthenga wotsiriza wochokera kumwamba. 
Adalivumbulutsa kwa Mtumiki womaliza Muhammad yemwe ndi 
Mtumiki wankulu kuposa atumiki onse a Mulungu amene adadza ndi 
uthenga wochokera kumwamba. 

Mulungu adatumiza kwa anthu atumiki wocthedwa 
MURSALINA, munyengo yosiyanasiyana, m'mayiko osiyanasiyana, 
ndiponso kumibadwo yosiyanasiyana. Maina ena a atumiki ndi awa: 

Adam. Nuhu, Ibrahim, Ishaka, Yaaqub, Yusuf, Musa, Daudi, 
Sulaiman, Yahya, ndi Isa (Yesu) 

Tsono ena mwa iwowa, adawavumbulutsila mabuku ake. Komatu 
uthenga wa mabukuwa udali wopita kumtundu wawo kapena ku 
m'badwo wawo wokha osati kwa anthu onse. Pachifiikwa chimenechi, 
uthengawu udaonongedwa ndi maganizo a wanthu poonjezera ndime 
zina ndi kuchotsa ndime zina zimene ankaziona kuti sizikuyenerana 
ndi nthawi yawo ndi m'badwo wawo. Ndipo mabuku ena amene 
wanthu akuwatcha kuti adavumbulutsidwa ndi Mulungu , kuchokera 
kumwamba, wanthu amenewa sangathe kusonyeza umboni woona 
kuti ndi ziganizo ziti za ndime zimene zidavumbulutsidwa kumwamba 
ndi zimene zidaonjezedwa pambuyo pake munthawi yosiyanasiyana. 
Pakuti mabukuwo Mulungu adawavumbulutsa kuti athandize 
panthawi yokhayo. 

Itatha nthawiyo adawalekerera sadawasunge kuti asasokonekere. 
"Koma Qur'an, yolemekezeka adaivumbulutsa kwa Mtumiki 
wotsiriza yemwe sipanatumizidwe pambuyo pake Mneneri ngakhale 
Mtumiki, kuti likhale Buku la anthu onse. Chifukwa chakuti 
sikudzabweranso Mtumiki wina. Ndipo adakwaniritsa ndi buku 
lopatulikali Chipembedzo Chake Choona. Ndipo adakwaniritsa ndi buku 
lakeri Chisomo chake pa wanthu ake onse ndipo adalichita kukhala 
chiongoko ndi kuunika mpaka pa tsiku lomaliza," 



VI 



Mulungu adalonjeza kuti adzalisunga buku lakeli (laQur'an) 
sipadzachotsedwa lemba kapena kuonjezera lemba ndiponso 
sipadzatheka kuonekamo zolakwika kapena kutsutsana ndi mabuku 
akale. 

Buku ili la Qura'n limene tili naloli, limene lafala pa dziko lonse la 
pansi tikhoza kunena motsimikiza kuti ndiwo mawu a Mulungu 
Wapamwambamwamba adawavumbulutsa kwa Mtumiki wake 
Muhammad (S.A.W) muzaka mazana khumi ndi anayi zapitazo. 

Monga adalonjeza kulisunga buku Lakeli, lidzasungidwabe 
mpaka kutha kwa dziko la pansi Ndipo mu ndime ya 9 ya Surati Hijiri 
Mulungu wanena kuti. "Ndithudi ife ndi amene tauvumbulutsa 
ulalikiwu (Qura'n iyi) ndipo ife ndi amene tidzausunga. 

Mwatsoka, anthu akukhulupirira kuti Chisilamu tsopano ndi 
Chipembedzo cha ASilamu okha. Ndipo Qur'an ndi buku lopatulika la 
Asilamu okha. Alinso ndi chikhulupiriro chakuti Muhammad ndi 
Mtumiki wa Asilamu okha muongoli wawo osati wa anhtu onse. 

Kudza ndi ganizo ili ndi kulifalitsa, kunachitika ndi anthu omwe 
sadali Asilamu. Adachita izi chifukwa chakunyansidwa chabe ndi 
chipembedzochi kapena kusadziwa mokwanira za chipembedzochi. 
Mulungu wapamwambamwamba akunena m'buku lake lomaliza kuti 
Muhammad (madalitso a Mulungu ndi mtendere wake zikhale pa iye) 
sadali ngati atumiki amene adatsogola, chifukwa chakuti iye yekha 
ndi amene adamtuma kwa anthu onse, kumitundu yonse, kumakungu 
onse oyera ndi akuda. Mundime ya 158 ya Surat Al-A'raf, Mulungu 
wanena kuti. "Nena (iwe Mneneri Muhammad) E, inu anthu ! 
Ndithudi ine ndi Mtumiki wa Mulungu kwa inu nonse, Mulungu 
yemwe ndi mwini ufumu wakumwamba ndi pansi, palibe 
wopembedzedwa mwachoonadi koma iye yekha. Iye ndi yemwe 
amapeleka Moyo ndi Imfa. 

Choncho mkhulupirireni Mulungu ndi Mtumiki Wake yemwe ali 
Mneneri Ummiyyu (wosadziwa kuwerenga ndikulemba) yemwe 
akhulupirira Mulungu ndi mawu ake Ndipo mutsatireni iye kuti 
mukhale oongoka." 

Kunena motsimikiza Asilamu akuyetsetsa kukwaniritsa udindo 
wawo popereka umboni woona ndikufalitsa kwa anthu onse. 
Chisilamu sichidadze kwa anthuakuti akuti kapena mtundu 
wakutiwakuti koma chidadza kwa anthu ndi mitundu yonse ya 
padziko lapansi .Tsono chatsalira kwa amene akufuna kudziwa 



VII 



choonadi, ndikuti achifunefune powerenga Qur'an ndikumvetsetsa 
uthenga wake wa Mulungu omwe ukupezeka mkati mwake, chifukwa 
chakuti Qur'an ndi mphatso ya uzimu imene apatsidwa anthu onse ndi 
Mulungu. 

Qur'an ikulankhula ndi anthu onse. Qur'an ndi uthenga wa 
Mulungu kwa anthu onse, kuti anthuwo apeze mtendere wa muyaya. 
Uthenga wa Mulunguwu , ukuyikira umboni ndikutsimikizira 
mauthenga onse amene Mulungu adawabvumbulutsira aneneri ake 
kuyambira Mtumiki Adamu mpaka Isa (Yesu) ndipo Qur'aniyi 
ikukwaniritsa uthenga Wake.Choncho uthenga wa Mulungu 
wakwanira ndi buku lomaliza ndi Mtumikinso uyu womaliza 

Arabu ndi anthu oyamba amene idawalankhula Qur'an, kotero kuti 
Qur'an idabvumbulutsidwa n'chilankhulo cha Chiarabu, pambuyo 
pake idamasulidwa mzilankhulo zosiyanasiyana. Adauzidwa Msilamu 
aliyense kuti agwire ntchito molimbika pofikitsa uthenga 
wachoonadiwu kwa anthu onse pano padziko lapansi. Ndipo Hisitole 
(mbiri yakale ) ikuyikira umboni kuti Asilamu adakwaniritsa udindo 
umenewu moyenerana. Adaufikitsa uthenga wa Mulunguwu mbali 
zonse padziko lonse lapansi. Adamasulira matanthauzo a Qur'an 
muzilankhulo zosiyanasiyana zimene zidali zodziwika nthawi 
imeneyo kuti anthu apeze phindu ndi malangizo amene akupezeka 
mQur'an makamaka amene sakudziwa chilankhulo cha Chiarabu kuti 
atsatire malamulo ake ndikuzipewa zimene yaletsa Kunena 
mwatsatanetsatane, buku limeneli ndi lofunika ku mtundu wa anthu 
chifukwa chakuti muli zonse zofunika pamoyo wamunthu; m'mene 
angakhalire payekha kapena ndi anzake ;m'mene angagwirire ntchito 
yake yomuthandiza pano padziko lapansi kapena pa tsiku 
lachimaliziro. Ndipo Munthu amene awerenga bukuli natsatira 
zophunzitsa zake, limuongolera ndi kumuunikira njira ya choonadi 

Sura yoyamba ndi surati Fatiha. Ndipo sura yotsiriza ndi surati 
Nasi. Mulungu adalibvumbulutsa bukuli kwa womaloza mwa aneneri 
ake kuti likhale buku lomariza kwa anthu ake onse,lomwe mkati 
mwake muli maphunziro othandiza anthu kuti apeze mtendere pano 
padziko la pansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndime zake zidatsika 
mosiyanasiyana malingana ndi zinthu zomwe zinkachitika m 'nthawi 
ya zaka (23) makumi awiri ndi zitatu za uneneri Wake Muhammad 
(S.A.W) 

Gawo Una lidatsika iye akukhala mu mzinda wa Makka. Ndipo 
lina lidatsika atasamukira ku Madina. Sura zomwe 



VIII 



zidabvumbulutsidwa ku Makka zimafotokoza maziko a 
chikhulupiliro, monga kukhulupilira Mulungu, Angelo, Mabuku, 
Aneneri ndi tsiku lachimaliziro. Tsono sura zomwe 
zidabvumbulutsidwa ku Madina zimafotokoza malamulo a 
chipembezochi. M'Qur'an mukupezeka nkhani zakale ndiponso 
mukupezeka nkhani za kutsogolo. 

KUTANTHAUZIRA QUR'AN M'CHICHEWA 

Chifukwa chakufunika kwa uthengawu kuti ufike kwa anthu onse, 
a Bungwe la Africa Muslim Agency adandipempha kuti ndimasulire 
Qur'an m'chichewa, ndicholinga chakuti amene sangathe kumvetsa 
uthenga wake m'chiarabu, aumve m'chilankhulo chawo cha 
Chichewa. Choncho ntchitoyi idagwirikadi kotero kuti munthu 
akawerenga bwinobwino akhoza kumva uthenga wa Mulungu 
m' Qur'an. Ndayetsetsa m'kutanthauzira kwanga mawu oyerawa kuti 
musakhale zolakwika zambiri, koma ntchito yogwira Munthu 
siilephera kupezeka zolakwika kupatula zochita za Chauta. Munthu 
ndi Munthu basi.Choncho ndikupempha aliyense amene angapeze 
zolakwika pakatanthauzidwe ka Qur'an kapena kasankhidwe kamawu 
oyerawa, kuti anditumizire ndi cholinga choti pomazatuluka bukuli 
kachiwiri muzakhale mopanda zolakwika zimenezo 

Pamene ndimagwira ntchitoyi, panali mabuku amene 
ndimathandizika nawo pakasankhidwe ka kutanthauzira koyenera kwa 
Qur'an, komanso anthu amene amandithandiza pakasankhidwe ka 
mawu oyenera m'chichewa. Mabukuwa ndi awa Tafsiri ya Jalalain, 
Tafsiri ya Ibn Kathiri, Al Muntakhab ndi Swafuat Tafaasiri. Ndipo 
Ntchito yotanthauzira inatha m'chaka cha 1987 pambuyo poigwira 
mzaka zitatu. Ndipo kuyambira nthawiyo kufikana m'chaka cha 1999 
yakhala ikuunikidwandi ma Sheikh akuluakulu m'dziko muno. 

Tikupempha Mulungu kuti ntchito imene tagwirayi, ailandire 
ndipo akatipatse mphoto yake pa tsiku lachimaliziro. Tikupemphanso 
kuti bukuli alichite kukhala lolandiridwa ndi anthu onse, ndipo kuti 
apereke madalitso kwa onse amene anathandiza kuti bukuli lituluke. 

Ine M'bale Wanu 
Sheikh Khalid Ibrahim 
P.O BOX 60166 
Blantyre 
MALAWI 



■ ,, ,„-,, ,-i.r,^, 



QUR'AN 
YOLEMEKEZEKA 

yotanthauzidwa 
m'chichewa 



Nyumba ya Mfumu Fahd 
yosindikizira Qur'an yopatulika 



Surat 1. AI-Fatihah Juzu 1 



> *>i 



) a£\A\ djj-*» 



Surat Al-Fatihah I 



Wfmm& M 



1. M'dzina la Mulungu 
Wachifundo Chambiri, Wachisoni. 

2. Kutamandidwa konse nkwa 
Mulungu Mbuye Wa zolengedwa 
zonse. 

3. Wa chifundo chambiri, Wa 
chisoni. 

4. Mwini tsiku lachiweruzo. 

5. Inu nokha 
tikukupembedzani, ndiponso Inu 
nokha tikukupemphani 
chithandizo. 

6. Tiongolereni kunjira 
yoongoka. 

7. Njirayaomwe 
mudawapatsa chisomo; Osati ya 
amene adakwiyiridwa (ndi Inu) 
Osatinso ya omwe adasokera 










Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 2 ^ ^' * OjiJi 3jj-» 




SURAT AL-BAQARAH II 




££&& 



Iyi ndi imodzi mwa sura zomwe zinavumbulutsidwa ku 
Madina pambuyo pakuti Mtumiki (Mtendere ndi madalitso a 
Mulungu zikhale naye) atasamuka ku Makka. 

Iyi ndi sura yaitali kwambiri m' Qur'an (Msafu) yopatulika 
malinga ndi m'ndondomeko wa sura. 

Surayi yafotokoza mwatsatanetsatane zomwe Surat Fatiha 
yafotokoza mwachidule. Ndipo ikuti Qur'an ndilo gwero la 
chiongoko, chilungamo. Ndipo yakambanso za Qur'an, chiyanjo 
cha Mulungu ndi amene Mulungu adawakwiyira. Ndipo 
ikunenetsanso za Qur'an kuti njoona ndi kuti malangizo ake 
ngoona okhaokha; mulibe chilichonse chokaikitsa. Kenako 
yapitirira nkumafotokoza kuti anthu, kumbali ya uthenga wa 
Qur'an, adali m'magulu atatu. Gulu loyamba ndilo lokhulupirira 
Mulungu kudzanso zinthu zosaoneka ndi maso. Hi ndilo gulu 
lopambana. Gulu lachiwiri ndilomwe lidakana Mulungu ndi 
kutsutsa zinthu zonse zosaoneka ndi maso. Hi ndilo gulu lotaika. 
Gulu lachitatu ndilo gulu la achiphamaso lomwe 
linkakhulupirira Mulungu ndi Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
wa Mulungu zikhale naye) ndi pakamwa chabe pomwe 
m'mitima mwawo mudalibe chikhulupiriro. 

M'suramu mwafotokozedwa malamulo ambiri pa 
chikhulupiriro, mapemphero, malonda, makhalidwe abwino, 
kumanga ndi kulekana ukwati, eda, ndi kulemba ngongole ndi 
malamulo ena ambiri onena za chipembedzo cha Chisilamu. 
Ndipo yapitiriza kufotokoza zachiyambi cha mtundu wa 
munthu, potchula nkhani ya Mneneri (Adamu) yemwe ndikholo 
lamtundu wa munthu, ndi momwe adapezera ulemu kwa Angero 
ndi zina zonse zimene zinamchitikira, pamene satana 
adamunyenga. Ndipo surayi yafotokozanso mwatsatanetsatane 
makamaka za ana a Israyeli poti iwo adakhalira limodzi ndi 
Asilamu mu mzinda wa Madina. Ndipo surayi ikuchenjeza 
Asilamu kuti achenjere ndi Ayuda omwe nthawi zonse 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 3 > ^jk-\ T o^aJi Sj^ 



chikhalidwe chawo nkukonda ziwembu, chinyengo, kuswa 
mapangano ndi zina zoipa kwambiri. 

M'suramu mulinso malamulo a Swaumu (kumanga), Haji, 
ndi kuchita Jihadi panjira ya Mulungu. Ndipo yafotokozanso za 
kuipa kwa malonda akatapira, pochenjeza kuti amene achita 
malondawa ndiye kuti akumenyana ndi Mulungu ndi Mtumiki 
wake. 

Kothera kwake surayi, yaalangiza Asilamu kuti azichulukitsa 
mapemphero, ndi kulapa kwa Mulungu. 

Surayi ikutchedwa "Baqara" pokumbutsa chozizwitsa 
chachikulu chomwe chidachitika m'nthawi ya Mneneri Musa 
pamene adaphedwa munthu wa mtundu wa Aisiraeli. Amene 
adamupha sadadziwike. Choncho, adakasuma kwa Musa kuti 
mwina iye angamzindikire wakuphayo. Ndipo Mulungu 
adamzindikiritsa Musa kuti awalamule kuti aphe ng'ombe 
yaikazi ndi kuti amkwapule wakufayo ndi gawo lina la 
ng'ombeyo potero auka mwachifuniro cha Mulungu nkuwauza 
yemwe adamupha. Ndikutinso chimenechi chikhale chisonyezo 
chakukhoza kwa Mulungu kuukitsa anthu ku imfa. Potero surayi 
idatchedwa Surat Baqara, (sura yang'ombe). 




Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



> frjfcl 



t S^iJl 5jj«- 



Surat Al-Baqarah II 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Alif-Ldm-Mim} 

2. Hi ndi Buku lopanda 
chipeneko mkati mwake; Ndi 
chiongoko cha (anthu) oopa 
Mulungu. 

3. Omwe amakhulupirira 
zosaoneka ndi maso (Monga 
Munda wa mtendere, Moto, 
Angero. Ndi zina zotere zomwe 
Mulungu ndi Mtumiki 
Adazifotokoza), amapemphera 
Swala moyenera, Ndiponso 
amapereka m'zimene tawapatsa; 

4. Ndi amene akukhulupirira 
zomwe zidavumbulutsidwa kwa 
iwe, ndi zomwe 
zidavumbulutsidwa kale iwe 
usadadze Nakhulupiriranso 
(motsimikiza) kuti Lilipo tsiku 
lomaliza. 






*^ii^- 






q^i^jii^U- 



Jb 



©JSJI 



®iffltfb&2$<^ 



jjliliy^jc^L^S^i 



®fcS^Sfe» 






Sura iyi yayamba ndi malembo a Alifabeti, monga A.L.M. kusonyeza kuti 
Qur'an yalembedwa ndi malembo amenewa omwe anthu amawagwiritsa 
ntchito m'zoyankhula ndi m'zolembalemba zawo. Uku ndikuuza osakhulupirira 
kuti abweretse buku iawo lolembedwa ndi malembo omwe akuwadziwawo 
pamene iwo amanena kuti Qur'an adangoipeka yekha Muhamadi (SAW) 
siidavumbulutsidwe ndi Mulungu. Choncho Mulungu adawatchalenja kuti 
alembe buku Iawo lofanana ndi Qur'an, koma adalephera, ndiponso 
ikufotokoza za chikhalidwe cha anthu olungama. 

Choncho, kulephera kwawo ndi umboni wosonyeza kuti Qur'an ndi buku 
lovumbulutsidwa ndi Allah. 



Surat 2. AI-Baqarah Juzu 1 



1 *>i 



t djiJi djj--» 



5. Iwowo (omwe ali ndi 
chikhalidwe chotere), ali 
Pachiongoko chochokera kwa 
Mbuye wawo, Ndipo iwowo ndi 
omwe ali opambana (Pokapeza 
ulemerero wapamwamba ku 
Minda ya mtendere). 

6. Ndithu amene sadakhulupirire, 
nchimodzimodzi kwa iwo 
uwachenjeze kapena 
usawachenjeze Sangakhulupirire. 

7. (Ali ngati kuti) Mulungu 
wawadinda Chidindo chotseka 
mitima yawo ndi makutu awo 
(kotero kuti kuunika kwa 
Chikhulupiriro sikungalowemo), 
ndipo M'maso mwawo muli 
chophimba (sangathe Kuona 
zozizwitsa za Mulungu); Choncho 
iwo adzalandira chilango chachikulu. 

8. Pakati pa anthu alipo (anthu 
achinyengo) Amene akunena: 
"Takhulupirira mwa Mulungu ndi 
tsiku lomaliza," pomwe iwo Sali 
okhulupirira. 

9. Akufuna kunyenga Mulungu 
ndi amene Akhulupirira, ndipo 
sanyenga aliyense koma okha, 
ndipo iwo sazindikira (kuti 
Akudzinyenga okha). 

10. M' mitima mwawo muli 
matenda; ndipo Mulungu 
wawaonjezera matenda. Choncho 
Iwo adzalandira chilango 
chopweteka chifukwa chakunena 
kwawo zabodza. 



Itfyt* 



** ii-r <K \ 





















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



^ * >» 



Y dyLS\ Ojj*> 



11. Ndipo akauzidwa kuti, 
"Musaononge padziko," 
amayankhakuti: "Ife ndife 
okonza." 

12. Dziwani kuti, ndithudi, iwo 
Ndiwo ali oononga (padziko); 
Koma sakuzindikira. 

13. Ndipo akauzidwa kuti, 
"Khulupirirani monga momwe 
anthu ena akhulupirira," 
akuyankha Kuti, "Kodi 
tikhulupirire monga momwe 
Zakhulupirira zitsiru?" Dziwani 
kuti, ndithudi, iwo ndi omwe ali 
zitsiru, Koma sakudziwa. 

14. Ndipo akakumana ndi 
amene akhulupirira, amanena, 
"Takhulupirira." koma akakhala 
Paokha ndi asatana awo, amati: 
"Ndithudi, Ife tili pamodzi nanu. 
Timangowachita chipongwe basi." 

15. Mulungu adzawalipira 
chipongwe chawocho. 
Ndikuwalekerera 
akungoyumbayumba (Kugwira 
njakata) m'kusokera kwawo. 

16. Oterewo ndi omwe 
asinthanitsa chiongoko ndi 
kusokera, koma malonda awo 
sadawapindulire Chilichonse, tero 
sadali oongoka. 

17. Fanizo lawo 
(achinyengowo) lili ngati (Anthu 






*€$&&£&$&; 



fi^K 









Surat 2. AI-Baqarah Juzu 1 



) *>i 



T *j*J\ tjj*' 



apaulendo afungatiridwa Ndi 
chimdima) omwe ayatsa moto; 
ndipo Pamene udaunika zomwe 
zidali M'mphepete mwawo, 
Mulungu Nkuwachotsera kuunika 
kwawoko nawasiya Mumdima 
osatha kuona. 

18. (Nakhala ngati) agonthi, 
abubu, Akhungu; ndipo 
sangabwererenso 
(Kuchiwongoko). 

19. Kapena (fanizo lawonso) 
lili ngati chimvula Chochokera 
kumitambo m'kati mwake 
Muukhala mdima, mphenzi ndi 
kung'anima, Naika zala zawo 
m'makutu mwawo chifukwa 
Chamkokomo ndikuopa imfa 
(pomwe kutero Sikungawathandize 
chilichonse). Ndipo Mulungu 
akudziwa bwinobwino za 
Osakhulupirira. 

20. Kung'anima kukuyandikira 
kutsomphola Maso awo; nthawi 
iliyonse kukawaunikira, Nkuyenda 
m'menemo (mkuunikamo). Koma 
Kukawazimira, nkuima. ndipo 
Mulungu akadafuna 
akadawachotsera kumva kwawo 
Ndi kuona kwawo. Ndithudi, 
Mulungu ngokhoza chilichonse. 

21. E inu anthu! Pembedzani 
Mbuye wanu yemwe adakulengani 
inu ndi omwe adalipo kale, kuti 


















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



8 



\ *>■» 



t ljL3\ 5jj-> 



mudzichinjirize (ku chilango cha 
Mulungu). 

22. (Mulungu) yemwe 
adakupangirani Nthaka kukhala 
ngati mphasa, ndi thambo Kukhala 
ngati denga; ndipo adatsitsa Madzi 
kuchokera kumitambo natulutsa 
ndi madziwo, zipatso 
zosiyanasiyana kuti chikhale 
chakudya chanu. Choncho 
Mulungu musampangire anzake 
Uku inu mukudziwa (kuti alibe 
Wothandizana naye). 

23. Ndipo ngati muli ndi 
chikaiko m'zomwe 
Tamvumbulutsira kapolo wathu 
(Kuti sizinachokere kwa Ife, koma 
wangopeka Yekha) tabweretsani 
sura imodzi Yolingana ndi 
Quraniyi (m'kayankhulidwe ka 
nzeru Ndi kayalidwe ka malamulo 
ake). Ndipo itanani athandizi anu 
(kuti akuthandizeni) kupatula 
Mulungu; ngati Inu mukunena 
zoona (kuti Qur'an Njopekedwa). 

24. Choncho ngati simutha 
(kubweretsa sura imodzi yonga ya 
m'Qurani) ndiye kuti Simudzatha. 
Choncho opani moto omwe 
Nkhuni zake ndi anthu (okanira) 
Ndi miyala (yamafano) umene 
wakonzedwera kwa 
Osakhulupirira. 

25. Ndipo auze nkhani 
yabwino amene akhulupirira 












®&m&>!&Q& 



<&L5 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



1 *>» 



Y SjiJl 5jj-- 



nachita ntchito zabwino 
(Molungama) kuti ndithu 
adzalandira minda ya Mtendere 
momwe mitsinje ikuyenda pansi 
pake ndi patsogolo pake. Nthawi 
iliyonse kumeneko akapatsidwa 
zipatso Ngati chakudya, adzakhala 
akunena: "Izi ndi zomwe 
tidapatsidwa kale," (Chifukwa 
chakuti) adzapatsidwa zipatso 
zofanana (m'maonekedwe ake Ndi 
zimene adapatsidwapo kale. Koma 
makomedwe ake ngosiyana). 
Ndiponso Akalandira m'menemo 
akazi oyeretsedwa (Kuuve 
wamtundu uliwonse); ndipo Iwo 
adzakhala m'menemo muyaya. 

26. Ndipo Allah sachita 
manyazi kuponya Fanizo la 
udzudzu ndi choposerapo (Pa 
udzudzu). Koma amene 
Akhulupirira akuzindikira kuti 
(Fanizolo) ndi loona ndi lochokera 
mwa Mbuye wawo. Koma amene 
Sadakhulupirire, akunena: "Kodi 
Allah akufuna chiyani Pafanizo 
lotereli?" (Allah) Amawalekerera 
ambiri kusokera ndi Fanizo lotere, 
komanso amawaongola ambiri ndi 
fanizonso lotere. Komatu 
sawalekerera kusokera nalo 
Kupatula okhawo opandukira 
chilamulo (chake); 

27. Omwe akuswa chipangano 
cha Allah pambuyo pochimanga 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



10 



\ *>i 



Y SjiJl 3jj^ 



(kuti adzachikwaniritsa; 
ndikutsatira Malamulo a Allah), 
ndiponso amadula (Chibale) 
chomwe Mulungu adalamula kuti 
chilumikizidwe, naononga padziko 
(Poyambitsa nkhondo ndi 
ziwawa); Iwowo ndi amene ali 
otayika. 

28. Kodi mungamkane chotani 
Allah chikhalirecho inu mudali 
akufa Ndipo Allah adakupatsani 
moyo (Nakuikani padziko 
lapansi)? Kenako Adzakupatsani 
imfa (ikakwana nthawi Yanu 
yofera). Kenako adzakuukitsani 
(Ndikukutulutsani m'manda). 
Ndipo Kenako mudzabwezedwa 
kwa lye (kuti Mukaweruzidwe 
pazomwe mudali kuchita). 

29. lye ndi Yemwe 
adakulengerani Zonse m'dziko 
lapansi, kenako adalenga Thambo 
nakonza thambo zisanu ndi Ziwiri. 
lye Ngodziwa chinthu Chilichonse. 

30. Akumbutse (anthu ako 
nkhani iyi) Panthawi yomwe 
Mbuye wako anati kwa Angelo: 
"Ine ndikufuna kuika Mdziko 
lapansi wondiimirira." (Angelo) 
adati: "Kodi muika m'menemo 
amene Adzidzaonongamo ndi 
kukhetsa mwazi, Pomwe ife 
tikukulemekezani ndi 
Kukutamandani mokuyeretsani?" 
(Allah) Adati: "Ndithudi, Ine 






% { 



9? WZ 



ua 






S 19 * 9» 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



11 



> *>i 



t SjiJl Ojj^> 



ndikudziwa Zimene 
simukuzidziwa." 

31. Ndipo (Allah) adaphunzitsa 
Adam Mayina a (zinthu) zonse; 
Nazibweretsa (zinthuzo) pamaso 
pa Angelo, Naati (kwa Angelo): 
"Ndiuzeni Mayina a zinthu izi 
ngati mukunena Zoona (kuti inu 
ndinu ozindikira Zinthu)?" 

32. (Angelo) adati: 
"Kuyeretsedwa nkwanu! Ife tilibe 
kuzindikira kupatula chimene 
Mwatiphunzitsa. Ndithudi, Inu 
Ngodziwa Kwambiri, Anzeru 
zakuya." 

33. (Allah) adanena: "E iwe 
Adam! : Auze Maina ake." Ndipo 
pamene adawauza Mayina ake, 
(lye) adati: "Kodi Sindinakuuzeni 
kuti Ine ndikudziwa Zobisika 
zakumwamba ndi pansi, ndiponso 
Ndikudziwa zimene mukuonetsera 
poyera Ndi zimene mukubisa?" 

34. Ndipo (akumbutse anthu 
ako nkhani iyi) Pamene tidawauza 
Angelo: "Mgwadireni Adam." 
Onse adamugwadira Kupatula 
Iblisi (Satana); anakana 
Nadzitukumula. Tero adali 
m'modzi Mwa osakhulupirira. 

35. Ndipo tidati : "E iwe 
Adam! Khala iwe Ndi mkazi wako 
m'mundamo (mu Edeni); Idyani 
m'menemo motakasuka paliponse 






®,^ ; W' 















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 12 S sjA-i 



T S^iJl 5jj-» 



Pamene mwafuna; koma 
musauyandikire Mtengo uwu 
kuopera kuti mungakhale Mwa 
oipa (odzichitira okha zoipa)." 

36. Koma Satana (Iblisi yemwe 
uja) Adawalakwitsa onse awiriwo 
(nanyoza Lamulo la Mulungu 
ndikudya mtengo Woletsedwawo), 
nawatulutsa mu Mtendere momwe 
adaalimo. Ndipo Tidawauza: 
"Tsikani (mukakhale padziko 
Lapansi) pakati panu pali chidani. 
Ndipo (tsopano) pokhala panu ndi 
pa Dziko lapansi, ndipo mukapeza 
Chisangalalo pamenepo Chanthawi 
yopimidwa." 

37. Ndipo Adam adalandira 
mawu kuchokera kwa Mbuye 
wake, (napempha chikhululuko 
Cha Allah kupyolera m'mawuwo), 
Ndipo (Mbuye wake) adavomera 
kulapa Kwake. Ndithudi, Iyeyo 
Ngolandira Kwambiri kulapa, 
Wachisoni. 

38. Tidati : "Tsikani 
m'menemo nonsenu; Ngati 
chitakufikani chiongoko 
Chochokera kwa Ine, ndipo amene 
adzatsate Chiongoko changacho, 
paiwo sipadzakhala Mantha. 
Ndiponso iwo sadzadandaula. 

39. "Koma amene 
sanakhulupirire Anatsutsa mawu 
athu, Iwowo ndiwo anthu a kumoto. 
M'menemo akakhalamo muyaya." 















«£SS»' 






Surat 2. AI-Baqarah Juzu 1 



13 



1 *>i 



t OjiJ* djj-* 



40. E inu ana a Israyeli! 
Kumbukirani Chisomo changa 
chomwe ndidakudalitsani Nacho, 
ndipo kwaniritsani pangano lanu 
nanenso Ndikukwanitsirani 
pangano langa Pa inu. Ndipo ine 
ndekha ndiopeni. 

41. Ndipo khulupirirani zimene 
ndazivumbulutsa, Zomwe 
zikuchitira umboni zimene muli 
nazo, Ndipo musakhale oyamba 
kuzikana; ndipo Musagulitse 
mawu anga ndi (zinthu za) Mtengo 
wochepa. Ndipo Ine ndekha 
ndiopeni. 

42. Ndipo musasakanize 
choona Ndi chonama; ndikubisa 
Choona uku mukudziwa. 

43. Ndipo pempherani swala 
moyenera Ndikupereka chopereka 
(Zakati), Ndipo weramani pamodzi 
ndi owerama. 

44. Kodi mukulamula anthu 
kuchita zabwino Ndi kudziiwala 
inu eni pomwe inu Mukuwerenga 
Buku? Kodi simuzindikira? 

45. Ndipo dzithandizeni (pa 
zinthu zanu) Popilira ndi 
popemphera swala. Ndithudi, 
swalayo ndiyolemera Kupatula kwa 
odzichepetsa. 

46. Omwe akutsimikiza kuti 
adzakumana ndi Mbuye wawo, 
ndikuti adzabwerera kwa lye. 












OJ\J\ 



" fill'" 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



14 



\ *>i 



Y oyJi 5jj-» 



47. E inu ana a Israyeli! 
Kumbukirani Chisomo changa 
chomwe ndidakudalitsani Nacho. 
Ndithudi, Ine ndinakuchitirani 
Zaufulu kuposa zolengedwa zonse. 

48. Choncho opani tsiku 
lomwe munthu Aliyense 
sadzathandiza mnzake ndi 
Chilichonse, ndipo 
sikudzavomerezedwa Kwa iye 
(munthuyo) chiombolo, ndiponso 
Silidzalandiridwa dipo kwa iye; 
ndipo iwo Sadzapulumutsidwa. 

49. Ndipo (kumbukirani) 
pamene Tidakupulumutsani kwa 
anthu a Farawo, Omwe 
adakuzunzani ndi chilango choipa; 
Adali kuzinga (kupha) ana anu 
achimuna Ndikuwasiya moyo 
achikazi. Ndipo M'zimenezo 
mudali mayeso aakulu Ochokera 
kwa Mbuye wanu. 

50. Ndipo (kumbukiraninso) 
pamene Tidailekanitsa nyanja 
chifukwa cha inu (Kuti muoloke 
pa mchenga wouma), potero 
Tidakupulumutsani ndi kuwamiza 
anthu A Farawo (pamodzi ndi iye 
mwini) uku Inu mukuona; 
(chomwe chidali Chizizwa 
choonekera). 

51. (Kumbukiraninso) pamene 
tidamulonjeza Musa (Mose) 
masiku makumi anayi (kuti 















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 15 \ ^jJb-t 



t S^aJi 3jj-*» 



Tidzampatsa buku la Chipangano 
Chakale patapita Masiku makumi 
anayi pambuyo Pakupulumuka 
kwanu ndikuonongeka kwa 
Farawo); kenako inu 
mudapembedza Mwana wa 
ng'ombe pambuyo pake, (iye 
Kulibe, atapita ku chipangano cha 
Mbuye wake). Ndipo inu muli 
ochita zoipa. 

52. Kenako 
tidakukhululukirani pambuyo 
Pazimenezo, kuti muthokoze 
(mtendere Wa Mulungu). 

53. Ndipo (kumbukiraninso) 
pamene Musa (Mose) tidampatsa 
buku Lolekanitsa choonadi ndi 
chonama kuti Inu muongoke 
(polilingalira ndi Kutsatira 
malamulo ake)." 

54. Ndipo (kumbukiraninso) 
pamene Musa (Mose) Adanena 
kwa anthu ake kuti "E inu anthu 
Anga! Ndithudi, inu mwadzichitira 
nokha zoipa Pompembedza mwana 
wa ng'ombe. Choncho lapani kwa 
Mlengi wanu, Ndipo phanani 
nokha (amene ali Wabwino aphe 
oipa). Kutero ndi bwino Kwa inu 
pamaso pa Mlengi wanu." 
Choncho wavomera kulapa kwanu. 
Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa 
Mochuluka, Wachisoni. 

55. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) pamene Mudati: "E iwe 



q&M#6 



&*$&&$£&& 



a <:?'<& 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 16 > tjA-i 



T SyLJt Ojj~> 



Musa (Mose)!; 

Sitingakukhulupirire iwe mpaka 
Timuone Mulungu 
masomphenya." Ndipo Nkokomo 
wa moto udakugwirani Uku inu 
mukuona. 

56. Kenako tidakuukitsani 
kuimfa Pambuyo pakufa kwanu, 
Kuti muyamike. 

57. Ndipo tidakuphimbani ndi 
mthunzi Wamitambo (pamene 
mudali kuoloka Chipululu cha 
mchenga), ndipo Tidakutsitsirani 
mana ndi salwa, Ndi kukuuzani: 
"Idyani zinthu zabwino Izi zimene 
takupatsani." Komatu Sadatichitire 
Ife choipa koma adali Kudzichitira 
okha zoipa. 

58. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) pamene Tidati: 
"Lowani m'mudzi uwu, ndikudya 
M'menemo motakasuka paliponse 
pamene Mwafuna; ndipo lowerani 
pachipata Chake uku mutawerama 
(kusonyeza Kuthokoza Mulungu) 
ndipo nenani "E Mbuye wathu! 
Tikhululukireni Machimo athu". 
"Tikukhululukirani Machimo anu 
ndikuwaonjezera (mphoto 
Yaikulu) ochita zabwino." 

59. Koma anthu oipa adasintha 
(lamulo la Mulungu, nanena) 
mawu ena osati Amene 
adawuzidwa; (choncho adalowa 









\*'*9 "Mi\\ 9 ~ 9\<*\*<' J*'*.*" 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



17 



1 *jk-\ 



Y Sjiil 3jj-*» 



Uku akukhwekhwerera ndi matako 
awo). Tero Anthu oipawo 
tidawatsitsira mliri Wochokera 
kumwamba, chifukwa 
Chakutuluka kwawo m'chilamulo 
cha Mulungu. 

60. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) Pamene Musa (Mose) 
adapemphera anthu Ake madzi 
kwa Mulungu (atagwidwa ndi 
Ludzu loopsa m'chipululu), tidati: 
"Menya mwala ndi ndodo 
Yakoyo." (Atamenya), anatulukadi 
M'menemo akasupe khumi ndi 
awiri. Potero fuko lililonse 
lidadziwa malo Awo omwera. (Izi 
zidachitika kuti Asakangane). 
Choncho idyani, ndiponso Imwani 
muriziki (zopatsa) la Mulungu 
(Popanda inu kulivutikira), ndipo 
musasimbwe Padziko uku 
mukuononga. 

61. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) Pamene mudati: "E! 
iwe Musa (Mose)! Sitingathe 
kupirira ndi chakudya Chamtundu 
umodzi (chomwe ndi mana ndi 
Salwa); choncho tipemphere kwa 
Mbuye Wako kuti atitulutsire 
(atipatse) ife Zimene nthaka 
imameretsa, monga Masamba, 
nkhaka, adyo, nyemba Za mtundu 
wa chana ndi anyezi." lye adati: 
"Kodi mukufuna kusinthitsa 
Chonyozeka (choipa) ndi 
chabwino? Pitani m'midzi, ndipo 



6£*3&fBtfc&S»& 






®< 



~^S9 9 J 9S9 . 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 18 \ *jk-\ 



Y oyJl 5jj-** 



kumeneko mukapeza Zimene 
mwapemphazi" potero 
adapatsidwa Kunyozeka ndi 
kusauka; nabwerera ndi Mkwiyo 
wa Mulungu. Zimenezo 
n'chifukwa Chakuti iwo sadali 
okhulupirira Zisonyezo za 
Mulungu, ndikuti adali kupha 
Aneneri a Mulungu popanda 
chifukwa. Zidali tero chifukwa cha 
kunyoza kwawo, Ndipo adali 
olumpha malire. 

62. Ndithu, amene akhulupirira 
(Aneneri akale), Ndi Ayuda, ndi 
aKhirisitu ndi Sabayi; Aliyense 
waiwo amene akhulupirire 
Mulungu (Tsopano, monga 
momwe akunenera Mneneri 
Muhammadi {SAW}) 
nakhulupiriranso za tsiku 
Lomaliza, uku akuchita ntchito 
zabwino, Akalandira mphoto yawo 
kwa Mbuye wawo. Paiwo 
sipadzakhala mantha, ndiponso 
Sadzadandaula. 

63. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi, inu Ayuda) pamene 
tidalandira chipangano Chanu (kuti 
mudzagwiritsa ntchito Zomwe zili 
m'buku la Taurat), ndipo 
Tidakweza pamwamba panu phiri 
(La Sinai; tidati kwa inu:) 
"Gwirani Mwamphamvu chimene 
takupatsani, ndipo Kumbukirani 
zili m'menemo (pozigwiritsa 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



19 



\ *>» 



T oyaJl 5jj-»> 



Ntchito. Ndiponso musazinyozere) 
kuti Mukhale oopa Mulungu." 

64. Komapambuyo 
pazimenezo mudatembenuka 
Ndikunyoza. Pakadapanda ufulu 
wa Mulungu ndi chifundo chake 
pa inu, Mukadakhala mwa otayika 
(oonongeka Padziko lapansi). 

65. Ndithudi mudawadziwa 
anthu amene mwainu Adapyola 
malire pakuswa Kupatulika kwa 
Tsiku la sabata (m'mene 
tidawalangira Chifukwa chosodza 
nsomba patsiku Loletsedwa). 
Ndipo tidati kwa iwo: "Khalani 
anyani onyozeka." 

66. Ndipo tidakuchita kukhala 
anyaniko, Chilango chochenjeza 
amene Adalipo pa nthawiyo ndi 
akudza Pambuyo pawo, ndiponso 
Phunziro kwa oopa Mulungu. 

67. (Kumbukiraninso nkhani 
iyi, inu Ayuda) Pamene Musa 
adauza anthu ake: "Ndithudi, 
Mulungu akukulamulani kuti 
Muzinge ng'ombe." Iwo adati: 
"Kodi Ukutichitira zachibwana?" 
lye Adati: "(Sichoncho). 
NdikudzitchinjirizaNdi Mulungu 
kukhala mwa anthu aumbuli." 

68. Iwo adati: "Choncho 
tipemphere kwa Mbuye wako kuti 
atifotokozere bwino Mtundu wa 
ng'ombewo." lye adati "Ndithudi 















>&c&&$M>&t»i®z 






WMifKi 



Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 1 20 M *j^ y 



t IjLlS Ijj^i 



lye akunena kuti ng'ombeyo 
simkota kapena Mthanthi, koma 
yapakatikati pa zimenezi. Tero 
chitani zimene mukulamulidwa." 

69. Iwo adatinso: "Tipemphere 
kwa Mbuye Wako kuti 
atilongosolere maonekedwe Ake a 
ng'ombeyo." (Musa) adati: "lye 
Akuti ng'ombeyo ikhale yachikasu 
Kwambiri, yowakondweretsa 
oiwona." 

70. Iwo adatinso: "Tipemphere 
kwa Mbuye Wako kuti 
atilongosolere mmene Khalidwe 
lake lilili. Ndithudi, Ng'ombe 
zimene wafotokozazo n'zofanana 
kwa ife. Ndipo ndithudi, Mulungu 
akafuna Tikhala oongoka." 

71. Adati: "Ndithudi lye akuti, 
imeneyo ndi n'gombe 
Yosaigwiritsa ntchito yolima 
m'nthaka, Ndiponso yosathirira 
mbewu; yabwinobwino Yopanda 
banga." Iwo adati: "Tsopano 
Wabweretsa (mawu a) choonadi." 
Choncho Adaizinga, koma 
padatsala pang'ono kuti Asachite 
(lamulolo). 

72. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) pamene Mudapha 
munthu, kenako mudakangana ndi 
Kukankhirana chifukwa cha 
(munthuyo, ena Ankati uje ndiye 
wapha. Pomwe ena ankati koma 









9 &jj$"*'' 6 M-** 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



21 



S *>l 



X 5^aJ| 5jj-j 



Uje ndiye wapha). Ndipo Mulungu 
atulutsira Poyera zimene mudali 
kubisa. 

73. Choncho tidati: 
"Kwapulani thupi la Wakufayo ndi 
gawo la nyamayo. (Potero auka 
ndikunena za amene adamupha)." 
Momwemo Mulungu adzawaukitsa 
akufa (M'manda monga 
adamuukitsira wakufayo pamaso 
Panu), ndipo akukusonyezani 
zizindikiro Zake kuti mukhale ndi 
nzeru. 

74. Koma mitima yanu idauma 
pambuyo Pazimenezo; (ikhala 
gwa!), ngati Mwala kapena 
kuposerapo. Ndithudi Pali miyala 
ina yomwe Mitsinje ikutuluka 
mkati mwake; Ndipo pali ina 
imene imang'ambika Nkutuluka 
madzi mkati mwake; ndipo Pali 
ina imene imagwa chifukwa Cha 
kuopa Mulungu. (Koma inu Ayuda 
Simulalikika ngakhale mpang'ono 
Pom we). Ndipo Mulungu sali 
Wonyalanyaza zimene mukuchita. 

75. Kodi (inu Asilamu) 
mukuyembekezera Kuti 
angakukhulupirireni (Ayudawo) 
Pomwe ena a iwo ankamvera 
mawu A Mulungu, kenako 
nkuwasintha Pambuyo 
powazindikira bwinobwino,Uku 
akudziwa? 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



22 



\ *>» 



T SyUl Sjj-** 



76. Ndipo akakumana ndi 
amene Akhulupirira, amanena: 
Takhulupirira (kuti uyu, 
Muhammadi {SAW}Ndi mneneri 
woona, ndipo watchulidwa 
M'Mabuku athu)." Koma akakhala 
Kwa okha kuseli, amati: 
"Mukuwauza Iwo (Asilamu) 
zimene Mulungu 
Anakufotokozerani (M'buku la 
Taurat) kuti Adzakhale ndi mtsutso 
pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi 
mulibe nzeru? 

77. "Kodi sadziwa kuti 
Mulungu Akudziwa zomwe 
akubisa ndi Zomwe akuonetsera 
poyera? (Kwa Mulungu palibe 
chobisika). 

78. Ndipo mwa iwo 
(Ayudawo) zilipo mbuli 
Zosadziwa kuwerenga buku (la 
Mulungu), Koma ziyembekezero 
Zabodza basi, ndipo iwo alibe 
china Koma zakungoganizira basi. 

79. Chilango cha ukali 
chidzatsimikizika Pa amene 
akulemba buku ndi manja awo, 
Kenako nanena: "Hi lachokera kwa 
Mulungu," (akunena bodzalo) kuti 
apeze Zinthu za mtengo wochepa 
(za m'dziko Lapansi): 
Kuonongeka kuli pa iwo Chifukwa 
chazomwe manja awo alemba, 
Ndipo kuonongeka n'kwawo 
Chifukwa chazomwe adapeza. 















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 23 ^ *jk* 



t S^aJI 5jj-j 



80. Ndipo akunena: 
"Sudzatikhudza moto Kupatula 
masiku owerengeka basi."Auze: 
"Kodi mudapangana naye 
Mulungu, kuti potero sadzaswa 
lonjezo Lake, kapena 
mukungomunenera Mulungu 
Zimene simukuzidziwa?" 

81. Sichoncho! Komaamene 
wachita Choipa, ndi 
kuzunguliridwa Ndi machimo ake, 
otero ndi Anthu a kumoto. 
M'menemoAdzakhala muyaya. 

82. Ndipo amene akhulupirira 
nachita zabwino, Iwowo ndiwo 
anthu akumunda wa mtendere. 
M'menemo adzakhala muyaya. 

83. Ndipo (akumbutse nkhani 
iyinso) pamene Tidalandira 
pangano lamphamvu la ana A 
Israyeli kuti: Musapembedze 
aliyense Koma Mulungu; ndipo 
muwachitire zabwino Makolo anu 
ndi achibale anu, ndi amasiye,Ndi 
masikini (osowedwa); ndipo 
nenani Kwa anthu mwaubwino; 
ndipo pempherani Swala moyenera 
ndi kupereka Zakati Kenako 
mudatembenuka monyozera 
kupatula Ochepa mwainu, ndipo 
inu ndinu onyozera. 

84. Ndipo kumbukirani 
pamene tidalandira pangano Lanu 
kuti simukhetsa mwazi wanu, 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 24 ^ *j^ 



t djiJi djj-*» 



kutinso Simudzawatulutsa anthu 
anu m'midzi yanu, Ndipo inu 
munavomereza zimenezi, ndipo, 
Inu mukuikira umboni zimenezi 
(Koma simudatsate malamulowo). 

85. Tsono inu nomwe ndi 
amene mukuphana Ndikuwatulutsa 
ena a inu m'nyumba 
zawo;Mukuthandiza adani anu 
powachitira (Abale anu masautso) 
mwauchimo ndi Molumpha malire. 
Koma akakudzerani Akaidi, 
mukuwaombola, pomwe 
nkoletsedwa Kwainu kuwatulutsa. 
Kodi mukukhulupirira Mbali ina 
ya buku, mbali ina nkuikana? 
Choncho palibe mphoto kwa 
ochita izi Mwainu koma kuyaluka 
pamoyo wa padziko Lapansi; 
ndipo tsiku la chiweruzo 
Adzalowetsedwa ku chilango 
chaukali. Ndipo Mulungu sali 
wonyalanyaza zimene mukuchita. 

86. Iwowo ndi amene 
asinthanitsa Moyo wa tsiku 
lomaliza ndi Moyo wadziko 
lapansi Choncho 
sadzawachepetsera chilango, 
Ndiponso sadzapulumutsidwa. 

87. Ndithudi Musa tidampatsa 
buku (la Taurat) Ndipo tidatsatiza 
pambuyo pake atumiki (Ena). 
Ndipo Yesu mwana wa Mariya 
Tidampatsa zizizwa zoonekera, ndi 



s 9} ' lift*?' ?2- 9 '2{ 






"9"9i S* t'9'\' ■ \S&\[ ^ 9 " 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 25 > *& 



t djAJl $JJ~» 



Kumulimbikitsa ndi Mzimu 
Woyera (Gabrieli). Nthawi 
iliyonse Akakudzerani mtumiki 
ndi chomwe Mitima yanu 
siikonda, mumadzikweza. Ena 
mudawatsutsa ndipo ena 
mudawapha. 

88. (Iwo) adati: "Mitima yathu 
yakutidwa, (Potero tikulephera 
kumvetsa ulaliki Wako, iwe, 
Muhammadi {SAW}. Iwo 
ngabodza Pazimene akunenazi). 
Koma Mulungu Wawatemberera 
chifukwa cha Kusakhulupirira 
kwawo. Tero n'zochepa Zimene 
akuzikhulupirira. 

89. Ndipo pamene buku 
lidawadzera (m'nyengo Ya 
mtumiki Muhammadi {SAW}) 
lochokera kwa Mulungu, loikira 
umboni zomwe zili Pamodzi ndi 
iwo (adalikana) pomwe Kale 
(lisadadze bukulo) adali kupempha 
Chithandizo kupyolera kwa 
mtumiki Wolonjezedwa 
chogonjetsera amene 
Sadakhulupirire. Koma pamene 
Chidawadzera chimene 
adachidziwa, (Qur'an) 
Adachikana. Choncho 
matemberero A Mulungu ali pa 
osakhulupirira. 

90. N'choipa zedi chimene 
agula Pogulitsa chisangalalo cha 
tsiku Lomaliza cha mitima yawo, 






>&£&&>£&%$$% 



®v£&r**' iiA 



*je 






^j\^^^i^^s^^^ 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



26 



> *jk-\ 



T djiJi djj^ 



ndi pokana Pawo zimene Mulungu 
adavumbulutsa, Chifukwa cha 
njiru basi kuti Mulungu Watsitsira 
chifundo chake amene wamfuna 
Mwa akapolo ake (amene sali 
m'Yuda). Potero adabwerera Ndi 
mkwiyo wa Mulungu kuonjezera 
Pamkwiyo wakale. Ndipo 
osakhulupirira Adzakhala ndi 
chilango chosambula. 

91. Ndipo akauzidwa (Ayuda): 
"Khulupirirani zimene Mulungu 
wavumbulutsa (Kwa mtumiki 
Muhammadi {SAW})" amanena: 
"Tikukhulupirira zimene 
zidavumbulitsidwa Kwaife." 
Ndipo amazikana zomwe Sizili 
zimenezo ngakhale icho chili 
Choona, chomwe chikuikira 
umboni kuona Kwa zomwe ali 
nazo pamodzi. Nena: "Nanga 
bwanji mudapha aneneri a 
Mulungu Kalelo ngati muli 
okhulupiriradi?" 

92. Ndipo adakudzerani Musa 
ndi Zisonyezo zotsimikizika, koma 
pambuyo Pake mudapembedza 
mwana wa ng'ombe, Ndipo potero 
mudali anthu Ochita zoipa 
kwabasi. 

93. Ndipo (kumbukirani nkhani 
iyi, inu Ana a Israyeli) pamene 
tidalandira Kwainu pangano 
lamphamvu, ndipo 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 27 > *& 



t 5yJl 5jj-»» 



Tidakukwezerani phiri pamwamba 
panu (Uku tikuti): "Gwiritsani 
mwamphamvu (Malamulo) amene 
takupatsani, ndipo Mverani." (I wo) 
adati: "tamva (mawu anu), Koma 
tikunyoza (tikukana lamulo lanu)." 
Ndipo adamwetsedwa m'mitima 
mwawo (Kukonda kupembedza) 
mwana wang'ombe Chifukwa cha 
kusakhulupirira kwawo. Nena: 
"N'choipa zedi chimene 
chikhulupiriro Chanu 
chikukulamulirani ngati inu Mulidi 
okhulupirira." 

94. Auze (Ayudawo): "Ngati 
nyumba Yomaliza kwa Mulungu 
njanu nokha, osati Anthu ena 
(monga momwe mukunenera), 
Ilakalakeni imfa ngati mukunenadi 
zoona." 

95. Koma sadzailakalaka 
(imfa) ngakhale pang'ono, 
Chifukwa cha zomwe manja awo 
adatsogoza (Chifukwa cha 
machimo adadzichitira). Ndipo 
Mulungu akudziwa Bwino za 
anthu oipa. 

96. Ndipo muapeza (Ayuda) 
kuti Ngokondetsetsa kukhala ndi 
moyo Wautali kuposa anthu ena, 
Kuposanso anthu amene 
akuphatikiza Mulungu (ndi 
mafano). Aliyense Waiwo 
amafuna apatsidwe moyo 






£*>*.&> 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



28 



\ *>» 



t djiJl djj-* 



wokwana Zaka chikwi chimodzi. 
Pomwe kupatsidwa Kwake moyo 
wautali sikungamuike kutali ndi 
Chilango. Ndipo Mulungu akuona 
zonse Zimene akuchita. 

97. Nena: "Amene akhale 
mdani wa Gaburieli (Chifukwa 
chobweretsa Chivumbulutso kwa 
Muhammadi {SAW}, iyeyo ndi 
mdani wa Mulungu). Ndithudi, iye 
Waivumbulutsa Qur'an mumtima 
mwako Mwachilolezo cha 
Mulungu. (Sadachite 
Mwachifuniro chake). (Qur'an) ndi 
Imene ikutsimikizira zomwe zidali 
Patsogolo pake, ndiponso ndi 
chiongoko Ndi nkhani yabwino 
kwa okhulupirira. 

98. Amene ali mdani wa 
Mulungu, ndi Angelo Ake, ndi 
Atumiki ake, ndi Gaburieli ndi 
Mikayeli (ndiye kuti akudzifunira 
imfa). Ndithu, Mulungu ndi mdani 
wa Osakhulupirira. 

99. Ndithu, tidavumbulutsa 
kwa iwe Zisonyezo zooneka. 
Ndipo palibe wozikana Koma 
okhawo opandukira chilamulo cha 
Mulungu. 

100. Kodi sizili tero kuti 
panthawi iliyonse Akupangana 
pangano lamphamvu, ena aiwo 
Akulitaya? Koma ambiri aiwo 
sakhulupirira. 



b$&i 






Ju^ 4t^\i J-*$ji Oi&Z* 



G¥ 9 >*\ \ 









Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 1 29 > *>' 



t o^iJl 5jj~> 



101. Ndipo pamene (Ayuda) 
adawadzera mtumiki Wochokera 
kwa Mulungu uku akuchitira 
umboni chomwe iwo ali nacho, 
gulu Lina mwa omwe adapatsidwa 
buku Adataya buku la Mulungu 
Kumbuyo kwa misana yawo ngati 
Kuti sakulidziwa. 

102. Adatsatira njira za afiti 
zomwe a Satana adali 
kuwafotokozera m'nthawi ya 
ufumu wa Sulaiman. Ndipo 
Sulaiman sadali mfiti, (sadasiye 
kukhulupirira Mulungu), Koma 
aSatana ndi amene 
sadakhulupirire, naphunzitsa anthu 
ufiti (umene adaudziwa kuyambira 
kale); natsatiranso njira za ufiti 
zimene zinatsitsidwa kwa Angelo 
awiri Haruta ndi Maruta (ku midzi 
ya) ku Babulo. Koma Angelo wo 
sadaphunzitse aliyense 
pokhapokha atamuuza kuti: "Ife 
ndife mayeso (ofuna kuona 
kugonjera kwanu malamulo a 
Mulungu); Choncho musamkane 
(Mulungu)." Komabe 
ankaphunzira kwaiwo njira 
zolekanitsira pakati pa munthu ndi 
mkazi wake, (ndi zina zotero). 
Ndipo sadavutitse aliyense ndi 
zimenezo koma mwachilolezo cha 
Mulungu. Ndipo akuphunzira 
zomwe zingawavutitse pomwe 
sizingawathandize. Ndithudi, 



6 &&&&&&%> 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



30 



> *>i 



T S^iJl Sj>*> 



akudziwa kuti yemwe wausankha 
(ufitiwo) sadzakhala ndi gawo 
lililonse (la zinthu zabwino) tsiku 
lomaliza. Ndithudi, nchoipitsitsa 
chimene adzisankhira okha 
akadakhala akudziwa. 

103. Ndipo iwo 
akadakhulupirira nadzitchinjiriza 
(ku zoletsedwa), ndithudi, mphoto 
yochokera kwa Mulungu 
ikadakhala yabwino kwaiwo, 
akadadziwa. 

104. E inu amene 
mwakhulupirira! musam'nenere 
(M'neneri liwu lakuti) "raina" 
(Ndicholinga chomunenera kuti 
iye ndi mbutuma) Koma 
mnenereni (liwu lakuti) 
"utiyang'anire", ndipo mverani 
Malamulo. Kwa osakhulupirira 
kuli chilango chopweteka. 

105. Amene sadakhulupirire 
mwa anthu amabuku (Ayuda ndi 
Akhirisitu) ndi omphatikiza 
Mulungu (Arabu), safuna kuti 
chabwino chilichonse chochokera 
kwa Mbuye wanu chitsitsidwe 
kwainu (Asilamu). Koma Mulungu 
amamsankhira chifundo chake 
amene wamfuna. Ndipo Mulungu 
ndi mwini chifundo chochuluka. 

106. Ay a (ndime) iliyonse 
yomwe tikuifafaniza kapena 
kuiiwalitsa (mumtima wako) 
Tikubweretsa yabwino kuposa iyo, 









(J*~«*d 46»J>^J &£?- 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 31 S *jJfc-i 



y djiS\ 5jj^» 



Kapena yofanana nayo. Kodi 
sukudziwa Kuti Mulungu 
ngokhoza chinthu Chilichonse? 

107. Kodi siudziwa kuti ufumu 
wakumwamba ndi Pansi ngwa 
Mulungu? Ndipo inu kupatula lye 
Mulungu mulibe mtetezi ngakhale 
Mthandizi. 

108. Kodi mukufuna kumfunsa 
mtumiki wanu (Inu Asilamu) 
monga momwe Musa (Mose) 
Adafunsidwira kale (mafunso 
achipongwe)? Ndipo amene 
angasinthitse chikhulupiriro ndi 
Kusakhulupirira, ndithudi 
wasokera njira Yolingana 
(yopanda majiga). 

109. Ambiri mwa amene 
anapatsidwa mabuku Akufuna 
kukubwezani (kukutembenuzani) 
Kuti mukhale osakhulupirira 
pambuyo pa Chikhulupiriro chanu 
chifukwa chadumbo Lomwe lili 
m'mitima mwawo (lomwe 
Lawapeza) pambuyo powaonekera 
choonadi Poyera. Choncho 
akhululukireni ndi Kuwasiya 
kufikira Mulungu adzabweretse 
lamulo Lake; ndithudi Mulungu 
ngokhoza chilichonse. 

110. Ndipo pempherani swala 
moyenera Ndiponso perekani 
Zakati. Ndipo chilichonse 
Chabwino chimene 



<J 9 c 






qj&Sjp 












Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 1 32 > *>■! 



X SjiJi 3jj-- 



mukudzitsogozera Mukachipeza 
kwa Mulungu. Ndithudi, Mulungu 
Akuona zonse zimene mukuchita. 

111. Eti akunena: "palibe amene 
adzalowe ku Munda wa mtendere 
koma amene ali Myuda Kapena 
Mkhirisitu." Zimenezo nzofuna 
Zawo chabe. Nena: "Bweretsani 
umboni Wanu ngati mukunena 
zoona." 

112. Ayi, koma amene nkhope 
yake yagonjera kwa Mulungu uku 
akuchita zabwino (kwa anthu 
Anzawo) iye ndi amene adzapeza 
mphoto yake Kwa Mbuye wake. 
Ndipo paiwo sipadzakhala Mantha, 
ndiponso iwo sadzadandaula. 

113. Ndipo Ayuda akumanena: 
"Akhrisitu alibe chilichonse 
(chotsamira pachipembedzo 
chawo);" naonso Akhrisitu 
akumanena: "Ayuda alibe 
chilichonse (chotsamira 
pachipembedzo chawo)," pomwe 
onsewa akuwerenga Buku 
(lomwe adawavumbulutsira 
popanda kutsatira zili m'bukulo). 
Mofanana ndi zoyankhula zawo, 
momwemonso akunena amene sali 
odziwa (Arabu opembedza 
mafano) monga zonena za Ayuda. 
Mulungu adzaweruza pakati pawo 
tsiku la chimaliziro pazomwe adali 
kusiyana. 






*£&' > fit % ><&'**«'<> L 99 'i 






Siirat 2. AI-Baqarah Juzu 1 33 > *jJfc-i 



t O^flJi OjJ-K 



114. Kodi alipo woipitsitsa 
woposa amene akutsekereza (anthu 
kulowa) m'misikiti ya Mulungu 
kuti lisatchulidwe m'menemo 
dzina lake nalimbika kuiononga 
(misikitiyo)? - Kotero kuti sikunali 
koyenera kwa iwo kulowa 
mmenemo koma mwa mantha. 
Kuyaluka kwapadziko lapansi 
nkwawo ndipo tsiku lomaliza iwo 
adzapeza chilango chachikulu. 

115. Ndipo kuvuma ndi 
kuzambwe nkwa Mulungu; ndipo 
pamalo paliponse pamene 
mwatembenukira, (pomwe 
Mulungu wakulamulirani kuti 
mutembenukire), pamenepo 
mupezapo chiyanjo cha Mulungu. 
Ndithudi Mulungu ngokwanira 
ponseponse, wodziwa chilichonse. 

116. Ndipo (osakhulupirira) 
akumanena: "Mulungu 
wadzipangira mwana." (Mulungu) 
wapatukana ndi zimenezo. Koma 
(zolengedwa) zonse za kumwamba 
ndi pansi nzake. Zonse 
zikumumvera lye. 

117. (lye ndi) Mlengi wathambo 
ndi nthaka popanda chofanizira. 
Ndipo akafuna chinthu kuti 
chichitike amangoti: "chitika," 
ndipo chimachitikadi. 

118. Ndipo aja osadziwa 
akunena: "Bwanji Mulungu 















M^*^$$2t& 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 34 \ ^\ 



Y $jiJ\ 3jj-- 



osatilankhula ife? Kapena 
kutibweretsera chizindikiro 
(chizizwa)?" Mofanana ndi 
zoyankhula zawozo adanenanso 
amene adalipo kale. Mitima yawo 
yalingana. Ndithu, Ife tazifotokoza 
zizindikiro momveka kwa anthu 
otsimikiza (m'chikhulupiriro). 

119. Ndithudi, Ife takutumiza 
(iwe Mtumiki {SAW}) Ndi 
choonadi kuti ukhale wouza 
nkhani zabwino, ndi wochenjeza. 
Ndipo siudzafunsidwa za anthu 
aku moto. 

120. Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu 
sangakondwere nawe pokhapokha 
utatsatira zipembedzo zawo. Nena: 
"Ndithudi, chiongoko cha 
Mulungu ndichomwe chili 
chiongoko chenicheni." Ngati 
utsata zilakolako zawo pambuyo 
pazomwe zakudzera, monga 
kuzindikira (kwenikweni), 
sudzapeza mtetezi aliyense 
ngakhale mthandizi kwa Mulungu. 

121. Anthu omwe tidawapatsa 
Buku naliwelenga; kuwerenga 
koyenera (kopanda kusintha mawu 
ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi 
amene akulikhulupirira (Bukuli la 
Qur'an). Koma amene angalikane 
iwowa ndi omwe ali oonongeka. 

122. E inu ana a Israyeli! : 
kumbukirani chisomo changa 















&tyo^&&&k 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 35 > ^ 



t 5jaJ' $jj-» 



chomwe ndidakudalitsani nacho. 
Ndithudi, ndidakuchitirani 
zabwino kuposa zolengedwa zonse 
(panthawi imeneyo). 

123. Ndipo opani tsiku lomwe 
munthu aliyense sadzathandiza 
munthu mnzake ndi chilichonse, 
ndipo dipo silidzalandiridwa, 
ndipo kuombola kwa owombola 
sikudzamthandiza, ndiponso iwo 
sadzapulumutsidwa. 

124. Ndipo kumbukirani 
pamene Mbuye wa Ibrahim (Allah) 
adamuyesa iye mayeso ndi 
malamulo ambiri; ndipo iye 
adakwaniritsa. Adamuuza: 
"Ndithudi, Ine ndichita iwe 
kukhala mtsogoleri wa anthu." 
(Ibrahim adayankha kuti): "Kodi 
ndi ana anga omwe?" Adati: 
"(Inde; koma) lonjezo langa 
silingawafike Ochita zoipa." 

125. Ndipo (kumbukiraninso 
nkhani iyi) pamene tidapanga 
Nyumba (ya Al-Kaaba) kuti 
pakhale pamalo pobwelerapo 
anthu (poyendera anthu) 
ndikukhalanso malo achitetezo. 
Ndikuti pachiteni kukhala 
popemphelera Swala pamalo 
pomwe Ibrahim adali kuimilira 
(pomamga nyumbayo). Ndipo 
tidal amula Ibrahim ndi Ismail kuti: 
"Iyeretseni nyumba yanga 



®<*$\&&&$s$& 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



36 



\ >>» 



T 5jiJl 5jj-»» 



chifukwa cha oizungulira (pochita 
tawaf) ndi amene akuchita 
mbindikiro, ndi chifukwa cha 
Amene akuwerama ndi kulambira 
(kuswali Mmememo). 

126. Ndipo (kumbukirani nkhani 
iyi) Pamene Ibrahim adanena: "O! 
Mbuye wanga! : Uchiteni mzinda 
uwu (wa Makka) kukhala wa 
Chitetezo, ndipo zipatseni nzika 
zamunzindawu Zipatso amene 
akukhulupirira Mulungu Ndi tsiku 
lomaliza mwaiwo. Mulungu adati: 
"Nayenso wosakhulupirira 
ndinkondweretsa Pang'ono; 
kenako ndidzamkankhira ku 
chilango Cha mo to. Taonani 
kunyansa malo obwerera. 

127. Ndipo (kumbukiraninso) 
pamene Ibrahim ndi Ismaila 
ankakhazikitsa maziko a nyumba 
(Uku akupempha kwa Mulungu): 
"O! Mbuye Wathu! Tilandireni 
(ntchito yathuyi), Ndithudi, Inu 
ndinu Akumva; Odziwa." 

128. "O! Mbuye wathu! tichiteni 
kukhala ogonjera Inu, pamodzinso 
ndi ana athu muwachite kukhala 
Fuko logonjera Inu. Ndipo 
tidziwitseni (njira) Za 
mapemphero athu; ndipo 
tikhululukireni, Ndithudi, Inu 
ndinu wolandira kulapa 
Mochuluka; Wachisoni." 















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 37 \ *jJH 



t OjaJi 5jj-» 



129. "O! Mbuyewathu! 
Atumizireni mtumiki wochokera 
mwaiwo, kuti awawerengere ay a 
(ndime) zanu ndikuwaphunzitsa 
Buku (lanu) ndi nzeru ndikuti 
awayeretse. Inu ndinu Amphamvu 
zoposa, Anzeru zakuya." 

130. Kodi ndani wonyoza 
chipembedzo cha Ibrahim osati 
yemwe mtima wake uli wopusa? 
Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) 
padziko lapansi; ndipo iye Tsiku 
lomaliza adzakhala m'modzi wa 
anthu abwino." 

131. (Kumbukiraninso) pamene 
Mbuye wake adamuuza kuti: 
"Gonjera." (Iye) adati: 
"Ndagonjera kwa Mbuye 
wazolengedwa zonse." 

132. Ndipo Ibrahim 
adalangizanso ana ake zazimenezi, 
chonchonso Yakubu 
(adalangizanso ana ake kuti): "E 
inu ana anga! Ndithudi, Mulungu 
wakusankhirani chipembedzo; 
choncho musafe pokhapokha muli 
ogonjera Iye." 

133. Kodi inu (Ayuda ndi 
Akhrisitu) mudalipo pamene 
Yakubu idamdzera imfa. pamene 
adati kwa ana ake: "Kodi pambuyo 
panga mudzapembedza yani?" Iwo 
adayankha nati: "Tidzapembedza 
Mulungu wako, Mulungu 












','\ h g 91.9' * j, 9 *'? JS *if> \" 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 38 1 *j*-i 



t oyLJl 5jj-j 



wamakolo ako, Ibrahim, Isimail 
ndi Isihaka; Mulungu m'modzi 
basi. Ndipo ife tikugonjera lye. 

134. Umenewo ndi mbadwo wa 
anthu umene udamka Kale. 
Udzapeza zimene udachita, ndipo 
inunso Mudzapeza zimene 
mudachita. Ndipo inu 
simudzafunsidwa zimene iwo 
ankachita. 

135. (Iwo Ayuda) adati (kwa 
Asilamu): "Khalani Ayuda (ndipo 
mukhala oongoka)." (Naonso 
Akhrisitu adati): "Khalani 
Akhrisitu (ndipo mukhala 
oongoka)." Nena: "Koma 
(tikutsata) chipembedzo cha 
Ibrahim yemwe adaleka 
zipembedzo zopotoka, ndipo sadali 
mwa ophatikiza Mulungu ndi 
mafano." 

136. Nenani (inu Asilamu 
kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu): 
"Takhulupirira Mulungu ndi 
zimene adavumbulutsa kwa ife, 
ndi zimene zidavumbulutsidwa 
kwa Ibrahim, Isimail, Isihaka, 
Yakubu ndi zidzukulu (zake) ndi 
zimene adapatsidwa Musa, Yesu, 
ndiponso zimene adapatsidwa 
Aneneri (ena) kuchokera kwa 
Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati 
pammodzi wa iwo (koma onse 
tikuwakhulupirira). Ndipo ife 
tikugonjera lye." 












Surat 2. Al-Baqarah Juzu 1 



39 



S *j*-i 



Y 9jaA\ «jj-> 



137. Ngati akhulupirira (Ayuda 
ndi Akhrisitu) monga m'mene 
mwakhulupirira, ndiye kuti 
awongoka. Koma ngati 
akutembenuka (posakhulupirira) 
ndiye kuti iwo ali m'kukangana. 
Choncho Mulungu akuteteza 
kuzoipa zawo, ndipo lye 
Ngwakumva; Wodziwa. 

138. (Tsatirani) chiongoko cha 
Mulungu (Chisilamu). Kodi ndi 
ndani amene ali ndi chiongoko 
Chabwino kuposa Mulungu? 
Ndipo ife, lye yekha 
timupembedza. 

139. Nena (iwe Muhammad 
{SAW}kwa Ayuda ndi Akhrisitu): 
"Ha! Mukutsutsana nafe za 
Mulungu (ponena kuti bwanji 
wapereka uneneri kumbali yaife), 
pomwe lye ndi Mbuye wathu 
ndiponso Mbuye wanu? (Pamene 
mudali olungama adakupatsani 
uneneri. Ndipo pamene mudakhota 
adakulandani natipatsa ife). Ife tili 
ndi zochita zathu; inunso muli ndi 
zochita zanu, ndipo ife 
tikudzipereka kwathunthu kwa lye 
(Mulungu). 

140. Kodi mukunena (Ayuda) 
kuti Ibrahim, Ismael Ishag, Yaqub 
ndi zizukulu Anali Ayuda kapena 
Akhrisitu? Nena: "Kodi inu ndi 
odziwa kwambiri Kapena 
Mulungu?" Kodi ndiyani oipitsitsa 















Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



40 



t *>i 



t 0jaJ\ 5jj-* 



kwambiri kwa lye Koposa yemwe 
wabisa umboni Ochokera kwa 
Mulungu! Komatu Mulungu sali 
wonyalanyaza Pazimene 
mukuchita. 

141. Iwo ndi mbadwo wa anthu 
umene Udanka kale (palibe phindu 
Kuwanyadira iwo) udapeza zimene 
Udachita, ndipo inunso mudzapeza 
Zimene mudachita. Ndipo inu 
Simudzafunsidwa pazimene Iwo 
ankachita. 

142. Posachedwapa mbutuma za 
anthu Zikhala zikunena: "Nchiyani 
chimene Chawatembenula ku 
chibula chawo Chomwe akhala 
akulunjika nkhope zawo." Nena: 
"Kuvuma ndi kuzambwe Ndi kwa 
Mulungu amamuongolera Amene 
wamfuna kunjira yolunjika." 

143. Choncho takusankhani 
(inu asilamu) kukhala mpingo 
wabwino (wapakatikati) Kuti 
mukhale mboni pa anthu ndi kuti 
Mtumiki akhale mboni painu. 
Ndipo chibula (Choyang'ana mbali 
ya ku Yerusalemu) chomwe udali 
nacho sitidachichite koma Kuti 
timdziwitse (adziwike kwa anthu) 
Amene akutsata mtumiki, ndi 
yemwe Akutembenukira 
m'mbuyo. Ndipo ndithudi, Chidali 
chinthu chovuta kupatula kwa 
omwe Mulungu wawaongola. 
Ndipo nkosayenera Kwa Mulungu 



©<^t£^>u; 






t * 9% ' 3 * 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



41 



Y *>■» 



Y dyJl djj-*. 



kusokoneza Swala zanu Pakuti 
Mulungu Ngoleza kwabasi kwa 
Anthu. Ngwachifundo chambiri. 1 

144. Ndithudi, taona 
kutembenuzatembenuza Kwa 
nkhope yako (kuyang'ana) 
kumwamba. Choncho 
tikutembenuzira ku chibula 
chimene Ukuchifuna. Tero 
tembenuzira nkhope yako kumbali 
ya msikiti woyera (Al-kaaba). 
Ndipo paliponse pamene mulipo 
Yang'anitsani nkhope zanu 
kumene Kuli (msikitiwo). Ndithudi 
amene Adapatsidwa Buku 
akudziwitsitsa kuti chimenecho 
nchoonadi chochokera Kwa 
Mbuye wawo. Ndipo Mulungu 
Siwonyalanyaza zimene akuchita. 
(Koma Chilichonse 
chikulembedwa m'kaundula). 

145. Ndipo awo adapatsidwa 
Buku ngakhale Utabwera ndi 
chisonyezo cha mtundu Uliwonse 
satsata chibula chako, 









1 Apa akutanthauza kuti pamene takutsogolerani ku njira yolunjika, takulolani 
inu ampingo wa Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kukhala 
anthu olungama, kulungama kosapyola nako muyeso ndiponso kopanda 
kuchepetsa chinthu chilichonse chazauzimu, ndi chamoyo wapadziko lino 
lapansi. Mtundu wa Chisilamu ngwapakatikati mzokhulupilira zake zonse. 
Umalimbikira kugwira ntchito ya zinthu za mdziko ndiponso ya zinthu 
zauzimu mwakhama, chilichonse mwazimenezi amachilimbikira mosapyoza 
muyeso. Limeneli ndilo tanthauzo la "mtundu wapakatikati." Chisilamu 
sichiiekerera munthu mmodzi kuti apondereze anthu ambirimbiri; ndiponso 
sichilekerera anthu ambiri kusalabadira za munthu mmodzi. Zimenezi 
nchifukwa chakuti inuyo mukhale mboni pa anthu pano padziko lapansi, 
ndikutinso mudzakhale mboni paiwo patsiku la chiweruzo. Ndipo kuti Mneneri 
(SAW) adzakhale mboni painu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



42 



t >>i 



t d^AJi OjJ~» 



Ngankhalenso iwe sutsata chibula 
chawo. Ndipo ena a iwo sali 
otsatira chibula cha Ena (Akhrisitu 
satsata chibula cha Ayuda. Ndipo 
Ayuda satsata cha Akhrisitu). 
Ngati utsatira zofuna zawo, 
pambuyo Pakuti kwakudzera 
kudziwa ndiye kuti ukhala Mwa 
ochita zoipa. 

146. Aja amene tidawapatsa 
Buku akumuzindikira (Mtumiki 
Muhammad {SAW}) monga 
mom we Amawazindikirira ana 
awo. Koma ena mwa Iwo akubisa 
choonadi uku akudziwa. 

147. (Kuyang'ana ku Al-kaaba 
popemphera Swala Ndicho) 
Choonadi chomwe chachokera 
kwa Mbuye wako; choncho 
usakhale mmodzi Mwa openekera. 

148. Ndipo mpingo uliwonse 
udali ndi chibula (Mbali 
yoyang'ana popemphera) chimene 
Udali kuchilunjika. Choncho 
pikisanani pochita Zabwino. 
Paliponse pamene mukhala 
Mulungu Adzakubweretsani 
nonsenu pamodzi (patsiku la 
Chimaliziro). Ndithudi, Mulungu 
ngokhoza chinthu Chilichonse. 

149. Ndipo paliponse pomwe 
wapita tembenuzira Nkhope yako 
kumbali ya Msikiti Woyera 
(Panthawi yopemphera). 
Chimenecho Nchoonadi 












%*$s^M*0v>&x 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



43 



t *>» 



t S^aJI 5jj-*> 



chochokera kwa Mbuye wako. 
Ndipo Mulungu sali wonyalanyaza 
zimene Mukuchita. 

150. Paliponse pamene wapita 
(iwe Mtumiki) Tembenuzira 
nkhope yako kumbali Ya Msikiti 
woyera. Ndipo paliponse Pamene 
(inu Asilamu) Muli tembenuzirani 
nkhope Zanu kumbali yake (Ya 
Msikiti) kuti anthu asakhale Ndi 
mtsutso pa inu, kupatula Amene 
adzichitira zoipa mwa iwo. Tero 
musawaope, koma Opani Ine, 
ndipo ndikwaniritsa Chisomo 
changa pa inu kuti muongoke. 

151. Monganso tidamtumiza 
mtumiki kwa inu Wochokera mwa 
inu kuti akuwerengereni aya 
(Ndime) zathu, ndikukuyeretsani 
(kuuve Wopembedza mafano) ndi 
kukuphunzitsani Buku ndi nzeru, 
ndikukuphunzitsani Zimene 
simunali kuzidziwa. 

152. Choncho ndikumbukireni 
(pondithokoza Pamtendere umene 
ndakupatsaniwu.) Nanenso 
ndikukumbukirani (pokulipirani 
Mphoto yaikulu). Ndipo 
ndiyamikeni; Musandikane. 

153. E inu amene 
mwakhulupirira! Dzithandizeni 
(Pazinthu zanu) popirira, ndi 
popemphera Swala. Ndithudi, 









®$M$^%%>M 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



44 



X tjk-\ 



t o^iJl Sjj-u 



Mulungu ali pamodzi ndi opirira. 

154. Ndipo musanene za amene 
aphedwa pa Njira ya Mulungu kuti 
"ngakufa." Iyayi Ngamoyo, koma 
inu simuzindikira. 

155. Ndipo tikuyesani ndi 
chinthu choopsa (monga 
Nkhondo), njala, kuchepa kwa 
chuma, kutaika Kwa miyoyo ndi 
kuonongeka kwa mbeu. Tero auze 
nkhani yabwino opirira. 

156. Omwe mavuto akawapeza 
amati: "Ndithudi, Ife nga 
Mulungu, ndipo kwa lye ndiko 
Tidzabwerera." 

157. Otero ndi amene ali ndi 
madalitso ndi Chifundo 
chochokera kwa Mbuye wawo. 
Ndiponso iwo ndi amene ali 
oongoka. 

158. Ndithudi, Safaa ndi Marwa 
(mapiri awiri Omwe pakati pake 
pamachitika pemphero Loyenda 
ndawala) ndi zizindikiro 
Zolemekezera chipembedzo cha 
Mulungu. Choncho, amene 















^ 






5v 



1 M'ndimeyi Mulungu akulangiza Asilamu kuti akhale opirira pa masautso 
amtundu uliwonse amene akukumana nawo. Kupirira ndi chida chakuthwa 
chopambanitsa munthu ndi kugonjetsera masautso. Munthu wosapirira ndi 
zopweteka sangapambane pazofuna zake. Mulungu akutilangizanso kuti 
tifunefune chithandizo pochulukitsanso Swala chifukwa chakuti Swala 
imalimbikitsa mtima wa munthu pa masautso. Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye) ankati masautso akamkhudza amachita changu kukapemphera 
Swala. Ndipo ankatinso, "Mulungu waupanga mpumulo wanga kukhala mkati 
mwa Swala." 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



45 



t *>» 



t o^aJi i^y* 



akukachita mapemphero a Haji ku 
nyumbayo, kapena kuchita Umura, 
Sikulakwa kwa iye kuzungulira 
pamenepo (Pakati pamapiri 
amenewo). Ndipo Amene achite 
chabwino modzipereka 
(Adzalipidwa). Ndithudi, Mulungu 
Ngothokoza; Ngodziwa. 1 

159. Ndithudi, amene akubisa 
zimene tavumbulutsa Zomwe ndi 
zisonyezo zoonekera poyera, ndi 
Chiongoko pambuyo pozifotokoza 
Mwatsatanetsatane kwa anthu 
m'Buku, Mulungu 
akuwatemberera iwo. Ndiponso 
Akuwatemberera otemberera. 2 






1 Haji ndi Umura ndimapemphero amene sangachitike pamalo pena paliponse 
kupatula mumzinda wa Makka. Kachitidwe kamapemphero awiriwa 
nkofanana. Koma pamakhala kusiyana pang'ono pakati pa Haji ndi Umura. 
Kusiyana kwake kuli motere: Haji siichitika nthawi iliyonse koma m'miyezi 
yake yodziwika. Ndipo kutha kwamiyezi ya Haji ndi masiku khumi am'khumi 
loyamba am'mwezi wa Zuli Hija. Pomwe Umura ikhoza kuchitika m'mwezi 
uliwonse umene munthu wafuna. Pa Umura palibe chinthu chimodzi 
mwazinthu zomwe zimachitika m'mapemphero a Haji chomwe nkuimirira 
pamalo otchedwa Arafat. Koma zina zomwe zimachitika pamapempherowa 
nzofanana. 

Zofunika pamapemphero a Haji ndi Umura ndi izi> 

1. Kuzungulira Al-kaaba kasanu ndi kawiri (7) 

2. Kuyenda mwandawala kasanu ndi kawiri pakati pamapiri awiri omwe ndi 
Safaa ndi Marwa. 

3. Kumeta kapena kuyepula tsitsi. 

Pamapiripo Chisilamu chisanadze adaikapo mafano omwe anthu achikunja 
panthawiyo adali kuwapembedza. Tero pamene Chisilamu chidadza Asilamu 
ena sadali kuona bwino kukachitira mapemphero pamapiriwo poganizira 
zamafano amene adalipo kalelo. Koma adawauza kuti palibe kuipa kulikonse 
kuchitirapo mapemphero pamalopo chifukwa mafanowo adawachotsapo. 

2 Nkofunika kwa munthu aliyense amene wachidziwa choona kuchita izi:- 

a) Kuchivomereza choonacho. 

b) Kuchitsata. 

c) Kuchifalitsa. 

d) Kuchiphunzitsa. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 46 Y *jA-t 



T SjiJ* 5jj-» 



160. Kupatula amene alapa ndi 
kukonza (Zolakwika) 
nachilongosola (choonadicho Kwa 
anthu), iwowo ndi amene 
ndiwalandira Kulapa kwao. Ndipo 
ine Ngolandira kulapa Kwambiri, 
Ngwachisoni zedi. 

161. Ndithudi, amene 
sadakhulupirire, Namwalira ali 
osakhulupirira, pa iwo Pali 
matemberero a Mulungu, a Angelo 
ndi A anthu onse. 

162. M'menemo (m'chilango 
cha matemberero) Adzakhalamo 
mpaka muyaya. Ndipo chilango 
Sichidzapeputsidwa kwa iwo, 
ndipo Sadzapatsidwa nthawi 
(yopumula). 

163. Ndipo Mulungu wanu ndi 
Mulungu mmodzi Basi. Palibe 
wopembedzedwa mwachoonadi 
Koma lye. Ngwachifundo 
chambiri, Ngwachisoni. 1 












y%\MM&f4\M 



Choncho, masheikh ndi maulama ali ndi mwawi pokhala ndi ntchito 
yapamwambayi. Achite ntchitoyi modzipereka kwatunthu, mwaulere kapena 
molandira malipiro ngati alipo. Apitirize kuigwira ntchitoyi pamoyo wawo 
wonse ngakhale atakumana ndi zovuta pantchitoyi. Ntchitoyi njomwe aneneri 
a Mulungu adali kugwira. Tero aigwire motsanzira momwe aneneri a Mulungu 
adali kuigwirira ntchitoyi pamakhalidwe awo ndi machitidwe awo onse. Kubisa 
komwe kwanenedwa m'ndimeyi sikubisa mawu a Mulungu kokha, komanso 
kubisa maphunziro azam'dziko ofunika kwa anthu. 

Chisilamu chikulimbikitsa kuti ngati munthu akudziwa chilichonse chomwe 
chili ndi phindu kwa anthu awaphunzitse anzake, asawabise chifukwa choopa 
kuti nzeruyo angaitulukire anthu ambiri ndi kuti iye sadzapatsidwa ulemu 
kapena kuopa kuti ena angampose. Maganizo otere ngosafunika 
m'Chisilamu. 
1 Tanthauzo la ndime iyi ndikuti Mulungu wanu Wompembedza ndi mmodzi. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 47 Y *j£-i 



Y o^dJt 5jj~- 



164. Ndithudi, m'chilengedwe 
chathambo ndi Nthaka, ndi 
kusinthana kwa usiku ndi Usana, 
ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu 
Zikulu zomwe zikuyenda panyanja 
(Zitasenza zinthu) zothandiza 
anthu, ndi Madzi amene Mulungu 
Wawatsitsa kuchokera kumitambo, 
naukitsira Nawo nthaka pambuyo 
pokhala youma, Nawanditsa 
m'menemo mtundu uliwonse wa 
Nyama (chifukwa cha madziwo), 
ndi M'kusinthanasinthana kwa 
mphepo, ndi Mitambo yomwe 
yalamulidwa Kuyenda pakati 
pathambo ndi nthaka; Ndithudi, 
(m'mzimenezo) muli zisonyezo 
kwa Anthu anzeru, (kuti Mulungu 
alipo). 

165. Pali ena mwa anthu amene 
akudzipangira Milungu naifanizira 
ndi Mulungu. Amaikonda Monga 
momwe akadamkondera Mulungu. 
Koma Asilamu amene akhulupirira 









Alibe mnzake wothandizana naye; alibe mwana alibe mkazi ndipo alibenso 
makolo. Palibe wompembedza mwachoonadi padziko lonse lapansi 
ndikumwamba koma lye yekha. lye Ngwachifundo chambiri, Wachisoni kwa 
zolengedwa Zake; Woyera ndiponso Wotukuka pachikhalidwe Chake chonse. 
Ndipo ali kutali ndi zimene akumunenerazo. Kodi asatukuke chotani kuzimene 
akumunenerazo chikhalirecho lye ndi Yemwe adalenga thambo ndi zonse 
zam'menemo monga nyenyezi zikuluzikulu zomwe zikuyenda m'menemo 
mwadongosolo Lake lakuya popanda kuwombana ina ndi inzake. Ndipo 
m'dziko lapansi adaikamo zolengedwa zambiri zododometsa zomwe 
zikusonyeza mphamvu Zake zoposa, monga nyama zamoyo ndizomera 
zosiyanasiyana mtundu, Ndi zopanda moyo ndi chikonzero 

chawamphamvuyo. Ndipo zikuloza kuti alipo amene adazilenga ndi amene 
akuziyang'anira yemwe ndi Mulungu. Dongosolo lazinthuzi likusonyeza kuti 
Mulungu ndi mmodzi chifukwa chakuti pakadakhala anzake othandizana naye 
pakadakhala chisokonezo, wina akadafuna china pomwe wina akufuna china. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 48 t *>■» 



Y 5jA-Jl 3jj-- 



Amamkonda Mulungu koposa. 
Ndipo akadaona amene adzichitira 
zoipa Pamene azikachiona 
chilango (chomwe Awakonzera, 
akadaona zoopsa; Zosasimbika). 
Ndipo mphamvu zonse Nza 
Mulungu. Ndipo Mulungu 
ngolanga Mwaukali. 

166. (Akumbutse) nthawi imene 
otsatidwa Adzakana amene adali 
kuwatsata uku Atachiona chilango. 
Ndipo mgwirizano Wapakati pawo 
udzaduka. 

167. Ndipo otsatirawo adzati: 
"Kukadakhala Kotheka kwa ife 
kubwerera (kumoyo Wapadziko) 
tikadawakana monga iwo 
Atikanira." Umo ndi momwe 
Mulungu Adzikawaonetsera 
zochita zawo kukhala Madandaulo 
awo. Ndipo iwo Sadzatulukanso 
kumoto. 

168. E inu anthu! Idyani 
zabwino zimene zili M'nthaka 
zomwe zili zololedwa; Ndipo 
musatsate mapazi a Satana. lye 
Kwa inu ndi mdani woonekeratu. 

169. lye akukulamulani kuchita 
zinthu Zoipa ndi zauve. Ndikuti 









»j£ 









1 E inu anthu! Idyani zamdziko lapansi zomwe zili zabwino zimene Mulungu 
wakulolezani ndipo musapenekere chilolezo chake. Musadye chinthu 
chosaloledwa monga kudya chinthu chawina m'njira yachinyengo. 
Musakhwathule chuma chamnzanu. 

Ndipo chenjerani ndi njira za Satana yemwe amakukometserani zoipa. 
Dziwani kuti iyeyu ndi mdani wanu monga adalili mdani watate wanu Adamu. 
Dziwaninso kuti iye salamula kuchita zabwino koma zoipa zokhazokha. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



49 



t *>i 



t djiJl 3jj-» 



Mumnamizire Mulungu 
pomunenera zimene 
Simukuzidziwa. 

170. Ndipo kukanenedwa kwa 
iwo (kuti): "Tsatirani zimene 
Mulungu wavumbulutsa;" 
Akunena: "Koma tikutsata zimene 
Tidawapeza nazo atate athu." Kodi 
Ngakhale kuti atate awo sadali 
kuzindikira Chilichonse ndiponso 
sadali oongoka? (Awatsatirabe)? 1 

171. Ndipo fanizo la amene 
sadakhulupirire (omwe 
Akulalikidwa mawu a Mulungu, 
ndi makani Awo) lili ngati (mbusa) 
yemwe akukuwira Ziweto zake ndi 
kuzikalipira pomwe izo Sizimva 
tanthauzo lamawu oitanawo, Koma 
kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) 
Ndi agonthi, abubu ndi akhungu. 
Tero Iwo sangazindikire. 

172. E inu amene 
mwakhulupirira! Idyani zinthu 
zabwino zimene Takupatsani, 
ndipo yamikani Mulungu ngatidi 
inu Mukupembedza lye yekha. 

173. lye akukuletsani (kudya) 
nyama Zakufa zokha, liwende, 



\t\fote 












Chikhulupiriro chamunthu kuti chikhale champhamvu ndi chopindula 
pafunika kuti achidziwe bwinobwino chimene akuchikhulupiriracho. 
Asangotsatira ndikuchikhulupirira chifukwa choti auje ndi auje adali 
kuchikhulupirira chimenecho. Zinthu zotere zimawasokeretsa anthu ambiri. 
Anthu ena amachikhulupirira chinthu chifukwa chakuti makolo awo adali 
kuchikhulupirira pomwe chinthucho chiii chachabe. 

Mulungu adatipatsa dalitso lanzeru kuti tizirigwilitsira ntchito pofuna choonadi 
chazinthu, osati kumangotsatira ngati wakhungu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



50 



Y tjtr\ 



V djiJ\ djy^ 












6\ 



nyama Yankhumba ndi nyama 
Yodulidwa poikuwira mayina 
Amafano kusiya Mulungu. Koma 
amene Wasimidwa (nadya 
choletsedwacho) popanda 
Kuchikhumba choletsedwacho ndi 
mosapyoza Muyeso palibe tchimo 
kwa iye. Ndithudi, Mulungu 
Ngokhululuka kwambiri, 
Ngwachisoni zedi. 1 

174. Ndithudi, amene akubisa 
zomwe Mulungu Adavumbulutsa 
m'buku (la Baibulo) M'malo 
mwake nasankha zinthu zamtengo 
Wochepa, iwo sadya china 
mmimba mwawo Koma moto basi; 
ndipo Mulungu Sadzawayankhula 
tsiku Lachimaliziro (mwachifundo 
Koma mokwiya); Ndipo 
sadzawayeretsa. Ndipo iwo 
Adzapeza chilango chopweteka. 2 



1 Apa Mulungu akutiuza kuti zinthu zinaizi nzoletsedwa kudya koma ngati 
munthu atavutika kwambiri ndi njala yofuna kufanayo, akumlola kuzidya 
pamuyeso wothetsa njalayo, osati mokhutitsa. 

Chimene chadulidwa pochitchulira dzina lomwe si la Mulungu monga nyama 
zomwe zikuzingidwira kukwanitsa maloto aazimu, kapena yomwe yazingidwa 
chifukwa chotsilika nyumba, kapena kutsilika midzi, ndi zina zomwe 
zikuzingidwa kuti eti Satana asawavutitse; zonsezi nzoletsedwa. 

2 Ibunu Abbas adati ndime iyi ikufotokoza za atsogoleri a Chiyuda monga 
Kaabi bun Ashirafi ndi Maliki bun Swaifi ndi Huyaye bun Akhatwabi. Anthuwa 
adali kulandira mphatso zambiri zochokera kwa anthu awo owatsatira. 
Pamene Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adampatsa 
uneneri iwo sadakhulupirire chifukwa choopa kuti sapeza mitulo yochokera 
kwa anthu awo. Tero anabisa kwa anthu za uneneri wa Muhammad 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) Apa mpamene Mulungu 
adavumbulutsa aya (ndime) iyi, yakuti "Ndithudi, amene akubisa zomwe 
Mulungu adavumbulutsa m'Buku (la Baibulo) m'malo mwake nasankha zinthu 
zamtengo wochepa iwo sadya china m'mimba mwawo koma moto basi". 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



51 



y *>i 



Y o^iJt 3jj-*> 



175. Iwo ndi amene asinthanitsa 
Kusochera ndi chiongoko 
Ndiponso chilango ndi 
Chikhululuko. Kodi Ndi chiyani 
chikuwachititsa Kukhala opirira 
ndi moto. 

176. Zimenezo nchifukwa 
chakuti Mulungu Adavumbulutsa 
Buku lake mwachoonadi (Ndipo 
iwo adalikana). Koma amene 
Asemphana m'Bukumo ali 
munkangano Wonkera nawo kutali 
kusiya choonadi 

177. Ubwino suli potembenuzira 
Nkhope zanu mbali yakuvuma Ndi 
kuzambwe (Popemphera Swala); 
koma ubwino Weniweni ndi 
(waomwe) Akukhulupirira 
Mulungu, Tsiku lomaliza, Angelo 
ndi Buku, ndi Aneneri; napereka 
Chuma, uku eni akuchifunabe, 
Kwa achibale ndi amasiye, Ndi 
masikini ndi apaulendo (omwe 
Alibe choyendera), ndi opempha, 
Ndikuombolera akapolo; 
napemphera Swala, napereka 
chopereka (Zakati); Ndi 
okwaniritsa malonjezo awo 
Akalonjeza, ndi opirira Ndi 
umphawi ndi matenda ndi 
Panthawi yankhondo. Iwo wo ndi 
Amene atsimikiza (Chisilamu 
chawo). Ndiponso iwo wo ndi 
Omwe ali oopa Mulungu. 









Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 2 52 * *jJH 



t o^iJl 5jj*- 



178. E inu amene 
mwakhulupirira! Kwalamulidwa 
Kwa inu kubwezerana molingana 
kwa ophedwa; Mfulu kwa mfulu, 
kapolo kwa Kapolo, mkazi kwa 
mkazi. Koma amene 
wakhululukidwa ndi M'bale 
wakeyo pachinthu Chilichonse, 
atsatire ndi kulonjerera dipolo 
Mwaubwino. (Nayenso wolipa) 
apereke kwa lye mwaubwino. 
Kumeneko ndikufewetsa Kumene 
kwachokera kwa mbuye wanu, 
Ndiponso chifundo. Ndipo amene 
alumphe Malire pambuyo paizi, 
iye Adzapeza chilango 
chopweteka. ! 



'<h% '*"*%*'+ 9*<9 9>Z < k V 



Apa akunena kuti, "mfulu kwa mfulu" kuthanthauza kuti aliyense amene 
wapha nayenso aphedwe. Sikuti aphe munthu wina m'malo mwake. 
Chisilamu chisanadze kudali kuponderezana zedi. Mfulu yochokera kufuko 
lapamwamba. Ngati atapha mfulu yafuko lapansi eni awakuphayo adali 
kukana kumpereka kuti aphedwe. M'malo mwake amapereka kapolo kuti 
ndiye aphedwe m'malo mwake. Kapolo wamfulu lapamwamba akapha kapolo 
wamfulu lapansi sadali kumpereka kuti akaphedwe. Amati; "Kapolo wathuyo 
ngwapamwamba pomwe wanuyo ngonyozeka. Choncho palibe kufanana 
pakati pa awiriwa." Ndipo ngati zitachitika motere kuti kapolo waonyozeka 
nkupha kapolo waodzitukumula, odzitukumulawa amakana kupha kapolo uja 
m'malo mwake amafuna mfulu yochokera kufuko lonyozekalo. Tero Kurani 
idaletsa machitidwe oterewa. Anthu onse ngofanana, palibe kusiyana pakati 
pawo. Amene wapha aphedwe yemweyo osati wina, ngakhale atakhala mfulu 
kapena kapolo. Hi ndilo tanthauzo la aya (ndime) imeneyi. 
Tsono gawo lina limene likuti "Koma amene wakhululukidwa ndi mbale 
wakeyo..." tanthauzo lake nkuti amene wamphera mbale wake 
akamkhululukira wakuphayo amlipiritse dipo landalama. Tero apa akumuuza 
iyeyo kuti ngati atamkhululukira m'bale wakeyo nangomulipiritsa ndalama, 
alonjerere dipolo mwaubwino. Nayenso wolipayo apereke mwaubwino. 
Asachedwetse mwadala namzunguzazunguza. Tsono gawo lachitatu landime 
yokhayokhayi likutiuza za chifundo chimene Mulungu watichitira potilekera ife 
eni kusankha chiweruzo pankhaniyi. 
Munthu yemwe amphera mbale wake akhoza kuchita izi: 
a) Kuuza Boma kuti liphenso yemwe adapha mbale wakeyo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



53 



r *>i 



t ljAS\ 5jj-*» 



179. Mkubwezerana kofanana 
muli kusunga moyo kwa inu, e!, 
Inu eni nzeru! Kuti 
Mudzitchinjirize (kumchitidwe 
ophana) 1 

180. Kwalamulidwa kwa inu 
kuti mmodzi wanu imfa 
ikamuyandikira, Ngati asiya 
chuma, Apereke malangizo (pa 
zachumacho) Kwa makolo ake 
awiri ndi Achibale ake, 
mwaubwino. Ichi nchilamulo Kwa 
oopa Mulungu. 

181. Ndipo amene asinthe 
malangizowo Pambuyo 
pakuwamva; Utchimo wake uli pa 
Amene akusinthawo. Ndithudi, 
Mulungu Ngwakumva; 
Ngodziwa. 3 



<$&M&J®8&$ 












b) Kapena kumlipiritsa dipo. 

c) Kapena kumkhululukira popanda kulipa chilichonse. 

Ndipo gawo lomaliza landimeyi akumchenjeza wokhululukayo kuti 
asangomkhululukira munthuyo pamaso pa anthu kenako nkumachita chiwembu 
mobisa. 

1 Muli moyo wabwino m'machitidwe abwino chifukwa chakuti potsata zimenezi 
aliyense adzakhala wotsata mwambo. Adzaopa kuti ngati apha mnzake 
nayenso aphedwa. Ngati achitira mnzake choipa nayenso amchitira choipa. 
Tero popewa zopwetekazo akhala ngati akusunga miyoyo ya anthu ena ndi 
wake womwe. 

2 Kale malamulo ogawira chuma cha masiye asanafotokozedwe adampatsa 
ufulu aliyense kuti alembe wasiya (will) pazachuma chakecho m'mene mwini 
angaonere. Wasiyawo ukhale m'njira yachilungamo yolingana ndi Shariya. 
Asachite chinyengo chamtundu uliwonse. 

3 Apa akuwachenjeza amene auzidwa wasiyawo kuti asasinthepo kanthu. 
Ndipo akunenetsa kuti ngati wasiyawo uwonongedwa ndiye kuti anthu omwe 
adalandira wasiyawo akhala ndi uchimo chifukwa chosintha wasiyawo. Koma 
ngati wasiyawo udalembedwa mopanda chilungamo, monga kuti iye adati 
"Chuma changa m'dzawapatse ana anga aamuna okha basi" nkusiya 
kutchulapo aakazi, apo Mulungu akuloleza olandira wasiyawo kuti aukonze 
ndikuwagawira ana onsewo mwachilungamo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



54 



T t-jir\ 



T OjiJl 9jj-- 






182. Ndipo amene waopa kuti 
mwini wakeyo (Wopereka 'will' 
kapena waswiya) Angapendekere 
kumbali yokhota kapena 
Kuuchimo, nalinganiza pakati 
pawo, palibe Tchimo kwa iye. 
Ndithudi, Mulungu ngokhululuka 
zedi, Ngwachifundo chambiri. 

183. E inu amene 
mwakhulupirira! Kwalamulidwa 
kwa inu kusala (Ramadhani) 
monga momwe Kudalamulidwira 
kwa anthu Akale, inu 
musadabwere kuti Muope 
Mulungu (popewa Zoletsedwa). 

184. (Kusalaku nkwa) masiku 
owerengeka. Koma amene akhale 
odwala mwa Inu kapena kukhala 
paulendo, (Namasula masiku ena), 
Akwaniritse chiwerengerocho 

NT masiku ena. Ndipo kwa amene 
Sangathe kusala chifukwa 
Chaukalamba apereke dipo 
lodyetsa Masikini. Ndipo amene 
achite zabwino Mwachifuniro 
chake, kutero ndibwino Kwa iye. 
Ndipo kusala (pamene 
Kukulolezedwa kumasula) 
Ndibwino kwa inu, ngati Muli 
odziwadi (kufunika kwa kusala). 1 



1 Amene sangathe kusala ndi awa:- 

a) Okalamba kwambiri omwe abwerera kuumwana, amene sangathe kupilira 
ndi njala 

b) Odwala amene sangathe kusala ndipo alibe chiyembekezo choti achira, 
monga amene ali ndi matenda a "Cancer" kapena "High Blood Pressure" 









- ' f< "' l? %^% 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



55 



X *jJM 



V 5yL)l 5jj-*» 



185. (Mwezi uwu 
mwalamulidwa Kusala ndi ) 
mwezi wa Ramadhani Womwe 
mkati mwake Qur'an 
Idavumbulutsidwa kuti ikhale 
chiongoko Kwa anthu ndi 
zizindikiro zoonekera Poyera 
zachiongoko. Ndikutinso ikhale 
cholekanitsa (Pakati pachoonadi 
ndi bodza) Ndipo mwa inu amene 
akhalepo (Pamudzi) M'mweziwu, 
amange. Koma amene ali 
wodwala, Kapena ali paulendo, 
akwaniritse Chiwerengero 
m'masiku ena (Cha masiku amene 
Sadasale). Mulungu akukufunirani 
Zofewa, ndipo sakukufunirani 
zovuta. Ndipo kwaniritsani 






kapena matenda a "Sugar". Anthu oterewa akuloledwa kusiya kumanga. 
Ndipo tsiku lililonse aliyense waiwo apereke chakudya choposera Vzkg. 
Chakudya chomwe anthu m'dzikomo amadya. Koma amene ali osauka 
asachite zimenezi. 

Mulungu amkhululukira pakuti Mulungu sakakamiza munthu kuchita chimene 
sangathe kuchichita. 

1. Tsono wodwala yemwe ali ndi chiyembekezo chochira. 

2. Ndi wapakati amene akuvutika ndi kusala. 

3. Ndi woyamwitsa amene akuona kuti azunzika akasala, onsewa sapereka 
dipo lija. 

Koma adzalipa masiku amene adamasulawo zikawachokera zovutazo 
monganso zilili ndi wapaulendo. Koma masheikh ena akuti wapakati ndi 
woyamwitsa nawonso apereke dipo lachakudya. Tero malangizo awanso 
tikhoza kuwatsata. 

Tsono kunena koti: "Ngati mutasala ndi bwino kwainu"... kukusonyeza kuti 
kumanga silamulo lomwe Mulungu watikakamiza kuchita lopanda phindu 
kwaife, koma nchinthu chothandiza kwa anthu, makamaka pathupi lathu. 
Ndipo kuonjezera apa, Mulungu, pa tsiku la chimaliziro, adzatipatsa mphoto 
yabwino. Masiku ano madokotala onse padziko lapansi akuvomereza kuti 
kusala kuli ndi phindu laltkulu kuthupi lamunthu. Ichi ndi chimodzi 
mwazizindikiro zosonyeza kuona kwa chipembedzo cha Chisilamu. 
Chinenere nkhaniyi papita zaka zoposa chikwi chimodzi ndi mazana anayi 
(1 ,400) ndipo tsopano omwe sali Asilamu akuvomereza. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



56 



t *>» 



t SjSJl djj-- 



chiwerengerocho Ndi 
kumlemekeza Mulungu Chifukwa 
chakuti wakutsogolerani 
Ndikutinso mukhale othokoza. ] 

186. Ndipo akapolo anga 
akakufunsa za ine, (Auze kuti) Ine 
ndili pafupi nawo. Ndimayankha 
zopempha zawopempha pamene 
Akundipempha. Choncho iwo 
ayankhe Kuitana kwanga ndipo 
andikhulupirire Kuti aongoke. 2 

187. Kwaloledwa kwa inu 
muusiku wosala Kukumana ndi 
akazi anu. Iwo ali ngati Chovala 
chanu. Inunso muli ngati chovala 
Chawo. Mulungu wadziwa kuti 
mudali Kudzichitira chinyengo 
nokha. Choncho Walandira kulapa 
kwanu ndipo Wakukhululukirani. 
Tsopano khudzanani nawo Ndipo 
funani chimene Mulungu 
wakulamulirani, Ndipo idyani ndi 
kumwa mpaka kudziwike 
Bwinobwino kwa inu kuyera kwa 
mbandakucha Ndi kuda kwa 









1 Mulungu akufuna kuti tikwaniritse chiwerengero chamasiku makumi atatu 
(30) kapena makumi awiri ndi mphambu zisanu ndi zinayi (29) chifukwa choti 
phindu lakumanga silingapezeke mthupi lamunthu pokhapokha kumangaku 
kutakwaniritsidwa m'masiku amenewa. 

Mulungu akufuna kuti timthokoze paufulu wakewu umene watichitira 
potilamula kuchita chilichonse chodzetsa chabwino kwaife ndikutiletsa 
zodzetsa mavuto kwa iye. 

2 Sikuti iwe wekha ndiwe uzipempha Mulungu kuti "Ndipatseni chakuti; 
nchiritseni kumatenda akutiakuti" pomwe iwe suvomera kuitana kwa Mulungu 
poleka zimene akukuletsa ndi kutsata zimene akukulamula. Yamba 
kumuvomera Mulungu usanayambe kumpempha ndiye kuti pempho lako 
lidzakhala laphindu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



57 



t *>» 



t SjaJi djj-- 



mdima wausiku; (kufikira Mdziwe 
kuti kucha kwalowa, usiku watha). 
Kenako kwaniritsani kusala mpaka 
dzuwa Litalowa. Ndipo 
musakhudzane nawo (akazi Anu) 
pamene inu mukuchita mbindikiro 
M'misikiti. Amenewo ndi malire a 
Mulungu; Choncho 
musaayandikire. Motere ndimo 
Mulungu akulongosola 
Mwatsatanetsatane zisonyezo zake 
kwa anthu Kuti akhale oopa 
Mulungu (potsatira malamulo Ake 
ndi kusiya zoletsedwa). 1 

188. Ndipo musadye chuma 
chanu Pakati panu Mwachinyengo 
Pochipereka kwa oweruza (M'njira 
ya ziphuphu) ndi cholinga Choti 
mudye gawo la chuma Cha anthu 
mwatchimo Uku inu mukudziwa. 

189, Akukufunsa zamiyezi 
Nena: "Imeneyi ndi miyeso 









•,i<*6,UiU 



&&>$-$\&-&&s 



1 Pachiyambi pomwe lamulo lakumanga lidakhazikitsidwa adawaletsa anthu 
kukumana ndi akazi awo usiku pambuyo poti iwo agona tulo ngakhale kuti 
angogona pang'ono pokha. Kukumana ndi mkazi akumane asanagone. Tero 
tamuloli lidali lovuta kwambiri kwa iwo kulitsata. Ena a iwo adalakwa 
pang'ono. Choncho kudalengezedwa kuti "Tsopano pali chilolezo choti 
akhoza kuchita chilichonse mpaka m'mbandakucha. Ndipo kunena koti 
"Funani chimene Mulungu wakulamulani" ndi kulilimbikitsa lamulo 
kuchilolezocho. Musati kuti poti kale adakuletsani kukumana ndi akazi anu 
pambuyo pogona tulo ndiye mupitiriza kutero - iyayi. Koma tsatirani 
chilolezocho. 

"Itikafu" ndikuchita chitsimikizo munthu chokhala mumsikiti kwamasiku akuti- 
akuti kapena nthawi yakutiyakuti. Ndipo pempheroli limachitika nthawi zambiri 
m'mwezi wa Ramadhani. akachita chitsimikizocho (niya) saloledwa kutuluka 
mumsikitimo pokhapokha patakhala chifukwa chachikulu chotulukira, monga 
kupita kukadzithandiza. Panthawi yoti munthu ali papemphero la Itikafu 
saloledwa kukumana ndi mkazi wake m'njira yaukwati ngakhale panthawi 
yomwe akupita kukadzithandiza. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



58 



1 *>-1 



t 6jiS\ 6jJ~- 



yanthawi Yozindikira anthu zinthu 
zawo Ndi nthawi ya Haji". Ndipo 
Siubwino kulowera m'nyumba 
Zanu mbali yakumbuyo kwake. 
Koma ubwino ndiyemwe Akuopa 
Mulungu. Ndipo lowerani 
M'nyumba podzera irf makomo 
ake. Opani Mulungu kuti inu 
mupambane. 1 

190. Ndipo menyani nkhondo pa 
njira ya Mulungu (Modziteteza) 
ndi amene Akukuthirani nkhondo. 
Koma Musalumphe malire 
(kumenya Amene sadakuputeni), 
chifukwa chakuti Mulungu 
sakonda olumpha malire. 2 

191. Ndipo apheni (amene 
akukuthirani nkhondo Popanda 
chifukwa) paliponse pamene 
Mwawapeza; ndipo atulutseni 
paliponse Pamene adakutulutsani; 
chifukwa Kusokoneza anthu pa 
chipembedzo chawo Nkoipitsitsa 
zedi kuposa kupha. Koma 
Musamenyane nawo pafupi ndi 
Msikiti Woyera pokhapokha 















%j» A** 



M'nthawi yaumbuli anthu ankati akalowa m'mapemphero a Haji sadali 
kulowa m'nyumba zawo podzera pakhomo. Ndipo sadalinso kutulukira 
pakhomo koma amaboola chibowo kuseri kwanyumba nkumalowerapo ndi 
kutulukirapo namaganiza kuti kutero ndimapemphero okondweretsa Mulungu. 
Tsono apa Mulungu akuletsa machitidwe amenewo. 

2 lyi ndiimodzi mwandime zomwe zikufotokoza bodza la amene akunena kuti 
Chisilamu chidafala ndi lupanga powathira anthu nkhondo mowapondereza 
kuti alowe m'chisilamu. 

Limeneli, ndithu, ndibodza lamkunkhuniza. Apa pakuonetsa kuti Mulungu 
akuwapatsa chilolezo Asilamu kuti amenyane ndi amene akuwaputa. Palibe 
chilolezo kwa iwo chomenyerana ndi anthu osawaputa. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 59 t *j*-i 



t 5yJi 5jj-*» 



atayamba ndiwo Kukumenyani 
pamenepo.Ngati atamenyana Nanu 
pamenepo, inunso menyananaoni. 
Motero ndi momwe ilili mphoto ya 
Osakhulupirira. 

192. Koma ngati asiya, ndithudi 
Mulungu Ngokhululuka, 
Ngwachifundo kwabasi. 

193. Ndipo menyananaoni 
kufikira pasakhale Masautso 
(ochokera kwa iwo powasautsa 
Asilamu popanda chifukwa). 
Ndipo Chipembedzo chikhale cha 
Mulungu (osati Kupembedza 
anthu).Koma ngati asiya, 
Pasakhale mtopola kupatula kwa 
okhawo Amene ali ochita zoipa. 

194. Mwezi wopatulika kwa 
mwezi wopatulika; Ndipo zinthu 
zopatulika paikidwa Kubwezerana. 
Ndipo amene wakuchitirani 
Mtopola, inunso mchitireni 
mtopola Molingana ndi momwe 
wakuchitirani Mtopola, ndipo 
opani Mulungu (musapyoze 
Kuposa momwe wakuchitirani). 
Ndipo Dziwani kuti Mulungu ali 
pamodzi ndi oopa. 

195. Ndipo perekani chuma 
chanu pa njira ya Mulungu, 
ndiponso musadziponye 
Kuchionongeko ndi manja anu; 
chitani Zabwino. Ndithudi, 
Mulungu amakonda Ochita 
zabwino. 












Surat 2. AI-Baqarah Juzu 2 



60 



t *>i 



t oyUl ^JJ- - 



196. Ndipo kwaniritsani Haji 
ndi Umura chifukwa Chofuna 
kukondweretsa Mulungu. (Izi zili 
Mkutsimikiza kulowa 
m'mapemphero a Haji). Ndipo 
ngati mutatsekerezedwa 
(kukwaniritsa Mapemphero), 
Choncho zingani nyama Zimene 
zili zosavuta kuzipeza (monga 
Mbuzi), ndipo musamete mitu 
Yanu kufikira nsembeyo ifike 
Pamalo pake pozingirapo (pomwe 
ndi pamalo Pamene 
mwatsekerezedwapo). Ndipo 
amene Mwa inu ali odwala kapena 
ali ndi zovutitsa Kumutu kwake, 
(nachita zomwe zidali Zoletsedwa 
monga kumeta) apereke dipo 
Lakumanga kapena kupereka 
sadaka , kapena Kuzinga nyama. 
Ndipo ngati muli pamtendere, 
Choncho amene adadzisangalatsa 
pochita Umura kenako nkuchita 
Haji, Azinge nyama imene ili 
Yosavuta kupezeka (monga 
mbuzi). Ndipo Amene sadapeze, 
asale masiku atatu konko Kuhajiko 
ndipo asalenso masiku Asanu ndi 
awiri mutabwerera Kwanu. 
Amenewo ndi masiku Khumi 
okwanira. Lamuloli nlayemwe 
banja Lake silili pafupi ndi Msikiti 
wopatulika. Ndipo Opani 
Mulungu, dziwani kuti Mulungu 
Ngwaukali polanga. 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



61 



1 *>i 



T 5jiJl 5jj-j 



197. (Mapemphero a) Haji ali 
ndi miyezi Yodziwika, (yomwe 
ndi: Shawali, Zuli Kada ndi Zuli 
Hija). Amene Watsimikiza kuchita 
Haji (m' miyezi) 
Imeneyo,asayankhule zauve, 
asachite Zauve, ndiponso 
asapandukire malamulo (Pochita 
zoletsedwa uku iye ali m'mape- 
Mphero a Haji), ndiponso 
asakangane ali M'Hajimo. Ndipo 
chabwino chilichonse Chimene 
mungachite, Mulungu achidziwa. 
Ndipo dzikonzereni kamba 
wapaulendo, ndithu Kamba 
wabwino (wadziko lapansi) ndi 
amene Angakupewetseni 
kupemphapempha. (Koma Kamba 
wabwino wa tsiku lomaliza ndiko 
kuopa Mulungu). Choncho 
ndiopeni inu eni nzeru. 

198. Sikulakwa kwa inu 
kufunafuna zabwino za Mbuye 
wanu (pogulitsa zinthu zanu uku 
Muli m'mapemphero a Haji, 
kapena kugula). Ndipo 
mukabwerera kuchokera ku Arafat, 
Tamandani Mulungu pamalo 
otchedwa Mashari Harami 
(Muzidalifa). Ndipo 
Mukumbukireni monga Momwe 
adakutsogolerani. Ndithudi, kale 
Mudali mwaosokera. 

199. Kenako yendani limodzi 
kuchokera pamalo Pamene 



edS8\ 






<jb>[j \ £oI> £-* tj-<&g I 






Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



62 



Y *>i 



Y 3jaJ* $jj~> 



akuchokerapo anthu onse (pomwe 
Ndi pa Arafat), ndipo pemphani 
Chikhululuko kwa Mulungu. 
Ndithudi, Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachisoni zedi. 

200. Ndipo mukamaliza 
mapemphero anu (tsiku La Idi 
komwe ndikuponya sangalawe, 
kuzinga Nyama zansembe, kumeta 
ndi kuzungulira Kaaba {Tawafu-li- 
Ifaza}), mtamandeni Mulungu 
Monga momwe mudali 
kutamandira makolo anu Kapena 
mtamandeni koposa.Ndipo alipo 
ena Mwa anthu amene akunena 
(kuti): "O! Mbuye Wathu! 
Tipatseni padziko lapansi:" Ndipo 
Iwo alibe gawo lililonse pa tsiku 
lomaliza. 

201. Ndipo alipo ena mwa iwo 
omwe akunena kuti: "O! Mbuye 
wathu! Tipatseni (mtendere) 
padziko Lapansi ndipo patsiku 
lomaliza Mudzatipatsenso 
zabwino, ndikutitchinjiriza ku 
Chilango chamoto!" 

202. Iwo ndi amene adzapeza 
gawo lazimene Adapata; ndipo 
Mulungu ngwachangu 
Pakuwerengera. 

203. Ndipo mtamandeni 
Mulungu m'masiku 
Owerengekawo. Koma amene 
wachita Changu pamasiku awiri 



/), 



a&i^&iu^iij-tDt 



<99 '199% < 



"Z9I9 '*~\<r< 



\f' £* h 9 ?~<> * <i 9^9 ' 






4 * 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 63 Y ^ 



Y S^iJl djj-*» 



okha (nabwerera Kwawo) palibe 
tchimo pa iye. Ndipo amene 
Wachedwerapo palibenso tchimo 
pa iye kwa Amene akuopa 
Mulungu. Choncho opani 
Mulungu, ndipo dziwani kuti kwa 
Iye nkumene 
Mudzasonkhanitsidwa. 

204. Ndipo mwa anthu alipo 
amene zoyankhula Zake 
zikukondweretsa (iwe) pano 
padziko Lapansi, (koma tsiku 
lomaliza kuipa kwake 
Kudzadziwika). Ndipo iye 
akutsimikizira Mulungu kuti 
akhale mboni pa zomwe zili 
Mumtima mwake pomwe Iye ndi 
wa makani kwambiri. 1 

205. Koma akachoka (kwa iwe) 
akuyenda padziko (Uku ndi uku) 
ncholinga chofuna kuyipitsapo ndi 
kuononga zomera ndi miyoyo. 
Komatu Mulungu Sakonda 
kuononga. 

206. Ndipo akauzidwa kuti: 
"Opa Mulungu", Akugwidwa ndi 
mwano womupititsa Kumachimo, 












Tanthauzo lake nkuti alipo ena mwa anthu omwe angakukometsere 
zoyankhula zawo ndikuthwa kwa lirime lawo pomwe iwo chikhalirecho 
akungoyankhula kuti apeze zinthu zam'dziko. 

Ndimeyi ikufotokoza za Al Akhnas bun Shariki yemwe amati akakumana ndi 
mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye), amatamanda ndi kusonyeza 
chikhulupiriro chabodza. Koma akachoka pamaso pa mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) amayenda padziko ncholinga choononga. 
Umo ndi momwe alili makhalidwe a anthu ena, amangokometsa mawu 
pomwe zochita zawo nzauve. Tero tichenjere ndi anthu otere. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 64 * *>» 



Y SjiJl Oj^-» 



choncho Jahanama Ikukwana kwa 
iye (Kuwuchotsa mwano 
wakewo); Aipirenji malo 
okonzeredwa. 

207. Pali wina mwa anthu 
amene Akugulitsa mzimu wake 
chifukwa Chofuna chiyanjo cha 
Mulungu; Ndipo Mulungu 
ngodekha Kwa akapolo Ake. 

208. E inu amene 
mwakhulupirira! Lowani 
m'chisilamu Chonse ndipo 
musatsatire Mapazi a Satana. Iye 
ndi mdani wanu Woonekeratu 
poyera. * 

209. Ndipo ngati mutaterezuka 
(Kuchimwa) pambuyo 
Pokudzerani zisonyezo Za 
Mulungu zoonekera poyera, 
Dziwani kuti Mulungu 
Ngwamphamvu zoposa; 
Ngwanzeru zakuya. 

210. Kodi pali china chimene 
Akuyembekeza osati Kuwadzera 
Mulungu m'mithunzi Ya mitambo 
ndi (kuwadzera) Angero; 
nkuweruzidwa chilamulo 
(Chakuonongeka kwawo)? 



©a#<£# 









E! inu amene mwakhulupirira! Inu eni mabuku, gonjerani Mulungu. Ndipo 
lowani m'Chisilamu kwathunthu posachisokoneza ndi chinachache. 
Mawuwa adanenedwa pamene Abdullahi bun Salaami adalowa m'Chisilamu 
yemwe adali mkulu wa chiyuda. lye adapempha chilolezo kwa mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti aziliremekezabe Tsiku la Sabata 
(la chiweru) ndi kuti aziwerenga mawu am'Taurati m'swala zake zausiku. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



65 



X *>-» 



X o^iJl 5jj*rf 



Komatu zinthu zonse 
zimabwezedwa Kwa Mulungu. 

211. Afunse ana a Israeli kuti 
Ndizizindikiro zingati zopenyeka 
Zomwe tidawapatsa? Komatu 
amene angasinthe chisomo Cha 
Mulungu pambuyo pomudzera, 
(Mulungu adzamulanga). Ndithudi, 
Mulungu ngolanga mwaukali. 

212. Moyo wapadziko lapansi 
wakometsedwa Kwa amene 
sadakhulupirire, ndipo 
Amawachitira Chipongwe amene 
Akhulupirira. Koma amene Aopa 
Mulungu adzakhala Pamwamba 
pawo tsiku la Chiweruzo, ndipo 
Mulungu Amapatsa amene 
wamfuna Popanda chiwerengero. 

213. Anthu onse adali ampingo 
umodzi (Wa Chisilamu panthawi 
ya Adamu kufikira Nuhi kenako 
Adayamba kupatukana), ndipo 
Mulungu Adatumiza aneneri 
Onena nkhani zabwino ndi 
Oteteza; ndipo pamodzi nawo 
Adavumbulutsa Mabuku 
achoonadi Kuti aweruzire pakati 
Pa anthu pazimene adalekana. 
Ndipo Sadalekane pazimenezo 
koma aja amene Adapatsidwa 
mabukuwo pambuyo Powadzera 
Zizindikiro zoonekera poyera, 
Chifukwa Chakuchitirana dumbo 
pakati pawo. Koma Mulungu 
adawaongolera amene 






U>!5 {&&** &&£* WS^I 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



66 



t >>i 



t S^iJl Ijj^ 



Adakhulupirira kuchoonadi 
chazomwe Adalekaniranazo, 
Mwachifuniro chake. Ndipo 
Mulungu amamutsogolera kunjira 
Yolunjika amene wamfuna. 

214. Kodi mukuganiza kuti 
mukalowa Kumunda wa mtendere 
pomwe Sanakudzereni masautso 
Olingana (ndiomwe) adawapeza 
Amene adamuka kale inu 
musanabadwe? Kusauka ndi 
matenda Zidawakhudza, ndipo 
adawanjenjemeretsa Koopsa 
kufikira Mtumiki pamodzi Ndi 
amene Adakhulupirira naye adati: 
"Chipulumutso cha Mulungu 
chibwera liti?" Dziwani kuti ndithu 
Chipulumutso Cha Mulungu chili 
pafupi! 1 

215. Akukufunsa kuti apereke 
chiyani? Nena: "Chuma 
chilichonse chimene 
Mungachipereke, (Chiperekeni) 
kwa Makolo awiri, achibale, kwa 
ana Amasiye, kwa osauka, ndi kwa 
apaulendo. Ndipo chabwino 
chilichonse chimene Mungachite, 
ndithudi, Mulungu akuchidziwa. 2 









1 Apa Mulungu akufotokoza kuti Msilamu aliyense adzapeza mavuto pokwaniritsa 
Chisilamu chake. Palibe chinthu chopindulitsa chimene chimangopezeka 
mofewa. Mavuto ndi amene amamkonza munthu kuti akhale olimba. 
Choncho, munthu asaganize kuti adzapeza chinthu chamtengo wapatali 
popanda kuchivutikira. 

Adafunsa izi lisanadze lamulo lakagawidwe kachuma chamasiye. Pamane 
lidadza lamulo lakagawidwe kachuma chamasiye lidaletsa kupereka chilawo 
(wasiya) kwa anthu owagawira chumacho. Nchifukwa chakuti aliyense waiwo 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



67 



t *>» 



t SyLJi 5jj-* 



216. Kwalamulidwa kwa inu 
kumenya Nkhondo ( Yotetezera 
chipembedzo Cha Mulungu) 
pomwe iyo (nkhondoyo) 
Njodedwa ndi inu. Komatu Mwina 
mungachide chinthu pomwe Icho 
chili Chabwino kwainu. Mwinanso 
mungakonde Chinthu pomwe icho 
chili choipa Kwainu. Koma 
Mulungu ndiyemwe Akudziwa. 
Ndipo inu simudziwa. 

217. Akukufunsa (zalamulo la) 
kumenya Nkhondo M'miyezi 
yopatulika. Nena: "Kumenya 
Nkhondo m'miyeziyo Nditchimo 
lalikulu. Komatu Kuwatsekereza 
anthu kuchipembedzo Cha 
Mulungu, ndi kumkana Mulungu, 
(ndi Kuletsa anthu) kumsikiti 
wopatulikawo, Ndi kutulutsa anthu 
m'menemo nditchimo Loposa kwa 
Mulungu. Ndipo kutsekereza anthu 
kuchipembedzo chawo nzoipa 
Kwabasi kuposa kupha. Ndipo 
sasiya Kumenyana nanu kufikira 
akuchotseni M' chipembedzo 
chanu ngati angathe. Ndipo 
mwainu amene atuluke 

m' chipembedzo Chake, kenako 
namwalira uku ali Osakhulipirira, 
iwo ndi omwe ntchito zawo 
Zaonongeka padziko lapansi 









Mulungu adampatsa gawo lakelake. Koma ngati munthu ukufuna kupereka 
chilawo (wasiya) pachuma chako, pereka wasiyawo iwe usanafe. Ndipo gawo 

lawasiyawo lisapyole pa 73. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



68 



Y *>l 



T SyLJl 3jj-*» 



mpaka Tsiku lomaliza. Ndipo iwo 
ndi Anthu akumoto. M'menemo 
adzakhalamo mpaka muyaya. 1 

218. Ndithudi, amene 
akhulupirira, Ndi amene asamuka 
namenyana Pa njira ya Mulungu, 
iwo ndi amene akuyembekezera 
Chifundo cha Mulungu. Ndipo 
Mulungu Ngokhululuka kwambiri, 
Ngwachisoni chochuluka. 

219. Akukufunsa zamowa ndi 
njuga. Nena: M'zimenezo muli 
masautso ndi uchimo waukulu, ndi 
zina zothandiza kwa anthu. Koma 
masautso ake ngakulu zedi kuposa 
zothandiza zake. Ndipo 
akukufunsa kuti aperekenji: Auze: 
"chimene chapyolerapo (Pazofuna 
zanu)". Umo ndi momwe Mulungu 
akukufotokozerani ma Aya 
(malamulo) kuti mulingalire. 

220. (Kuti muganizire zinthu) 
zam'dziko lapansi ndi (zinthu) za 
tsiku lomaliza. Ndipo akukufunsa 






QlxSKxi* 



'- &&z 









1 Omtsatira a Mneneri (maswahaba) anakumana ndi osakhulupirira padeti ya 
30, m'mwezi wa 9 pakalendala ya Chisilamu. Ena amaganiza kuti detilo la pa 
30 lidali la m'mwezi wa Rajabu omwe ngoletsedwa kuchitamo nkhondo. 
Tero Akuraishi adamnamizira Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale 
naye) kuti waswa ulemerero wamiyezi yopatulika. Ndipo adabwera 
kukamfunsa kuti: "Kodi ndimmene ukuchitira?" Umo ndi momwe Mulungu 
adawayankhira. 

2 Apa akufotokoza kuti masautso ndi mavuto omwe mowa ndi njuga 
zimadzetsa ngakulu zedi kuposa ubwino wake. Mowa umamchotsa munthu 
nzeru pomwe nzeru ndidalitso lalikulu kuposa chilichonse. Ndipo mowa 
umamuonongera munthu chuma ndi kumdzetsera matenda m'thupi mwake. 
Nayonso njuga nchimodzimodzi. Imawononga chuma ndi kuyambitsa chidani 
pakati pa anthu. Zonsezi zimadzetsa chisokonezo kumtundu wa munthu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



69 



t *>» 



t SyUi 5j^» 



za ana a masiye, Nena: 
"Kuwachitira zabwino ndiwo 
ubwino; ngati mutasakanikirana 
nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi 
abale anu; ndipo Mulungu 
akumdziwa woononga ndi wochita 
zabwino. Ndipo Mulungu 
akadafuna, akadakukhwimitsirani 
malamulo. Ndithudi, Mulungu 
Ngwamphamvu zoposa; 
Ngwanzeru zakuya. 

221. Ndipo musakwatire akazi 
opembedza Mafano Mpaka 
atakhulupirira. Ndithudi, 
mdzakazi Wokhulupirira 
(Mulungu) ngwabwino kuposa 
Mfulu yachikazi yosakhulupirira, 
Ngakhale itakukondweretsani. 
(Ndipo ana anu aakazi a 
Chisilamu) Musawakwatitse kwa 
amuna Osakhulupirira, mpaka 
akhulupirire. Ndipo kapolo 
wokhulupirira (Mulungu) 
Ngwabwino kuposa mfulu 
yosakhulupirira, Ngakhale 
ikukukondweretsani. I wo wo 
akuitanira kumoto. Koma Mulungu 
akuitanira kumunda Wamtendere 
ndi kuchikhululuko Mwalamulo 
lake. Ndipo lye akulongosola 
Mwatsatanetsatane ndime za 
mawu ake Kwa anthu, kuti athe 
kukumbukira. l 









Ndime iyi ikuletsa Asilamu kukwatirana ndi anthu osakhulupirira Mulungu 
kupatula Akhirisitu ndi Ayuda. Nkosaloledwa mwamuna wa Chisilamu 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



70 



Y ^>l 



Y SjiJl 5jj-*» 



222. Ndipo (iwo) akukufunsa za 
Kukhala malo amodzi ndi Azimayi 
panthawi imene Akusamba, auze 
(kuti): "Zimenezo ndizovulaza 
(Ndiponso ndiuve). Choncho 
Apatukireni akazi m'nthawi 
Yamatenda akumwezi, Ndipo 
musawayandikire mpaka ayere. 
Ngati atayera, kumananaoni 
Kupyolera m'njira yomwe 
Mulungu Wakulamulani. Ndithu, 
Mulungu Amakonda olapa, 
ndiponso Amakonda odziyeretsa. 

223. Akazi anu ali ngati minda 
yanu; Choncho idzereni minda 
yanu Mmene mungafunire; Koma 
dzitsogozereni zabwino Nokha, 
ndipo opani Mulungu, Ndipo 
dziwaninso kuti Mudzakumana 
naye. Ndipo auze nkhani Yabwino 
amene akhulupirira 

224. Ndipo kulumbirira kwanu 
Dzina la Mulungu musakuchite 
Kukhala chokuletsani Kuchita 
zinthu zabwino (Zam'Chisilamu) 
ndi kuopa Mulungu, ndi 
kuyanjanitsa Pakati pa anthu. 
Ndipo Mulungu Ngwakumva, 
Ngodziwa. 1 












kukwatira mkazi wopembedza mafano. Nkosaloledwa kuti mkazi wa 
Chisilamu akwatiwe ndi mwamuna wopembedza mafano. Koma mwamuna 
wa Chisilamu atha kukwatira mkazi wa Chikhrisitu kapena wa Chiyuda pomwe 
mkazi wa Chisilamu saloledwa kukwatiwa ndi mwamuna wa Chikhrisitu 
kapena wa Chiyuda. 

1 Munthu ngati atalumbira kuti sachita chakutichakuti monga kunena kuti, 
"ndikulumbira Mulungu sindidzakhudzana naye uje", asasiye kukamba naye 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



71 



1 *»>l 



Y 5^iJl 9jj~t 



225. Mulungu sangakulangeni 
Pakulumbira kwanu kopanda Pake, 
koma adzakulangani Chifukwa cha 
malumbiro Anu amene mitima 
Yanu yatsimikiza Mwamphamvu. 
Ndipo Mulungu Ngokhululuka 
Kwabasi, Ndiponso Woleza. 

226. Kwa omwe akulumbirira 
Kuti adzipatula kwa akazi awo, 
(Nyengo yawo) ayembekezere 
Miyezi inayi. Koma ngati 
Atabwerera (Nakhala pamodzi Ndi 
akazi awo), ndithudi Mulungu 
Ngokhululuka kwambiri, 
Ndiponso Ngwachisoni zedi. 1 

227. Ndipo ngati atatsimikiza 
Kulekana, Ndithudi Mulungu 
Ngwakumva, Ngodziwa. 

228. Ndipo akazi osiidwa 
(asakwatiwe) Ayembekezere 
mpaka kuyeretsedwa Kutatu 
kukwanire. Ndipo nkosafunika 
Kwaiwo kubisa chimene Mulungu 
walenga m'mimba zawo, ngati 
Akukhulupiriradi Mulungu ndi 
tsiku Lomaliza. Ndipo amuna awo 
Ali ndi udindo wowayenereza 












munthuyo chifukwa chakuti adalumbirira kusayankhulana naye. Koma 
ayankhulane naye pambuyo popereka dipo kwa masikini pazomwe 
adalumbirazo. 

1 Mwamuna akalumbira kuti sakhala naye pamodzi mkazi wake, tero mkaziyo 
ayembekezere nthawi yamiyezi inayi. Ndipo ngati nthawiyi ipambana 
asanakhalebe naye pamodzi, apite akamsumire kwa Kadhwi (mkulu wodziwa 
malamulo a Chisilamu). Ndipo Kadhwiyo akakamize mwamunayo kuti akhale 
naye pamodzi mkazi wakeyo, apo ayi, awalekanitse ngati izo zitalephereka. 
Sibwino kuvutitsana pakati pa anthu makamaka pakati pamwamuna ndi mkazi. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 | 72 | T »>i 



Y SyiJt 5jj-*» 



Kuwabwerera m' nthawi yomweyo *-££ &\y\S-j* &*d&$o£& 

ngati akufuna Kuchita chimvano. ' ~ $ 9 <" 

Nawonso azimayi ali ndi Zofunika ^V* 

kuchitiridwa (ndi amuna awo) 

monga M'mene ziliri kwa 

azimayiwo kuchitira amuna Awo 

mwachilamulo cha Shariya. Koma 

amuna ali ndi udindo okulirapo 

Kuposa iwo. Ndipo Mulungu 

Ngwamphamvu zoposa; 

Ngwanzeru zakuya. 1 

1 Mkazi ngati amsudzula ukwati saloledwa kukwatiwa ndi mwamuna wina 
mpaka eda yake ithe. Ndipo eda njosiyanasiyana kwa akazi. Edayi njotere 
kusiyana kwake: 

1. Mkazi akasiyidwa ali ndi mimba, pamenepo ndiye kuti eda yake imatha 
akangobereka. Pompo mwamuna wina akhoza kumkwatira. 

2. Ngati wosiidwayo ndi mkazi yemwe sadwala matenda akumwezi 

(a) chifukwa chakukalamba 

(b) kapena chifukwa chakuti sanakwane zaka zoyambira kudwala kumweziko 

(c) kapena chifukwa chakuti chilengedwe chake chili momwemo 

(d) kapena zifukwa zina zomwe zimachititsa kuti asadwale matenda 
akumwezi eda yawo onsewa ndimiyezi itatu. Asakwatiwe mpaka miyezi itatu 
ithe kuchokera patsiku lomwe adawasudzula. 

3. Ngati wosudzulidwayo ndimkazi wodwala matenda akumwezi, eda yake 
imatha akamaliza "khului" zitatu. Tsono tanthauzo lakhului maulama 
amamasulira mosiyanasiyana. Pamazihabi a Imam Shafii tanthauzo lake 
ndikuyeretsedwa kutatu (twahara zitatu). Choncho kuyeretsedwa kutatuku 
kukatha kuyambira pomwe adamsudzula, akhoza kukwatiwa. Koma 
pamazihabi a Kibazi tanthauzo lake ndikudwala kumwezi katatu (hizi zitatu). 
Kukatha kudwala kumwezi kutatu komwe kwachitika pambuyo pamsudzulo 
ndiye kuti akhoza kukwatiwa. Eda ngati siinathe mkazi saloledwa kukwatiwa. 
Ngati atakwatiwa ali mu eda ukwatiwo suvomerezeka. Ndiye kutinso nthawi 
yonse yomwe mkaziyo akukhala limodzi ndi mwamunayo akuchita naye 
chiwerewere. Ndipo amene akubadwa mu ukwati wotere ndi ana obadwira mu 
chiwerewere. Akazi omwe asiidwa ukwati akuwalangiza kuti asabise mimba 
kuti mwanayo adzadziwike tate wake. Ngati eda siinathe ndiponso ngati 
kuchuluka kwa twalaka mwamuna sadamalize, mwamunayo ali ndi ufulu 
wobwererana ndi mkazi ngati atafuna. Tero padzangofunika kupeza mboni 
ziwiri zoti zimdziwitse mkaziyo kuti wamuna wake wabwererana naye. 
Mkaziyo kapenanso abale ake saloledwa kukaniza zimenezo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



73 



t *jA-i 



t 5^aJ| 5jj-*» 



229. Mawu achilekaniro 
chaukwati (twalaka) (Omwe 
akupereka mwayi kwa mwamuna 
Kubwereranso kwa mkazi wake), 
ndiomwe Anenedwa kawiri. 
Kenako amkhazike (Mkaziyo) 
mwaubwino (ngati afuna 
kubwererana Naye) kapena 
alekane mwaubwino (ngati 
Atafunadi kumleka. Ndipo 
sangathe kubwererana Naye ngati 
atamunenera kachitatu mawu 
Achilekano pokhapokha 
atakwatiwapo poyamba Ndi 
mwamuna ndi kusiidwa ndi 
mwamunayo). Ndipo sizili 
zololedwa Kwa inu kuti mutenge 
(kulanda) chilichonse Chimene 
mudawapatsa (akazi anu) 
pokhapokha (Onse awiri) ngati 
akuopa kuti satha Kusunga malire 
a Mulungu (malamulo a Mulungu). 
Ngati muopa kuti sasunga malire 
A Mulungu, ndiye kuti pamenepo 
pakhala Popanda tchimo kwa iwo 
(mwamuna woyamba Ndi 
mkaziyu) kulandira (kapena 
kupereka) Chodziombolera mkazi. 
Awa ndiwo malire a Mulungu; 
choncho musawalumphe. Ndipo 
amene Alumphe malire a Mulungu 
(powaswa), iwowo Ndiwo anthu 
ochitazoipa. 1 






Apa akuletsa kumlanda kanthu mkazi kapena kumuuza kuti abweze 
(mahari) chiwongo akalangidwe nawo patsiku lachimaliziro. Pamalo pamodzi 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



74 



t *>» 



t SyLJl 3jj-* 



230. Tero ngati atamuleka (ndi 
Kunena katatu mawu achilekaniro, 
Choncho mkazi ameneyo) 
ngosaloledwa kwa iye pambuyo 
Pakutero, kufikira akwatiwe ndi 
Mwamuna wina. (Ngati mwamuna 
Winayo atamusiya), palibe 
Kulakwa kwa awiriwo 
kubwererana Ngati akuona kuti 
adzasunga Malire a Mulungu. 
Ndipo awa ndi Malire a Mulungu 
omwe Akuwalongosola kwa anthu 
odziwa. 

231. Ndipo pamene musiya 
akazi Powanenera mawu 
achilekaniro, Niiyandikira 
kukwana nyengo 
yachiyembekezero Chawo (eda 
yawo), abwerereni Mwaubwino; 
kapena lekananaoni mwaubwino, 
ndipo musawabwerere 
Mowavutitsa kuti mupyole malire 
A Mulungu (poswa malamulo 
ake). Ndipo amene achite 
zimenezo ndiye kuti wadzichitira 
yekha zoipa. Ndipo ndime za 
mawu a Mulungu Musazichitire 
chibwana. Ndipo Kumbukirani 
mtendere wa Mulungu umene uli 
pa inu; Makamaka chisomo 
Chokuvumbulutsirani Buku (La 
Qur'an) ndi kudziwitsidwa Nzeru 
zomwe akukulangizani nazo. 









pokha mpomwe pali povomerezeka mkazi kudziombola kwa mwamuna wake 
ngati mkaziyo njemwe wafuna kuti ukwatiwo uthe, ndiponso ngati palibe 
choipa chilichonse chomwe mwamunayo akuchita ndipo sangathe kukhala 
naye mwamtendere. Pamenepa ndiye kuti mkaziyo abweze chiwongo kuti 
adzichotsemo muukwati woterowo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



75 



Y ^jA-i 



t S^iJt 5jj-*> 



Ndipo opani Mulungu, Ndithudi 
dziwani kuti Mulungu Ngodziwa 
chirichonse. 1 

232. Ndipo akazi mukawanenera 
Mawu achilekaniro (Oyamba Ndi 
achiwiri), iwo nakwaniritsa 
Chiyembekezero chawo, choncho 
(Inu abale Amkazi), musawaletse 
Kukwatiwanso ndi amuna awo 
(Kubwererana) ngati pali 
chimvano Pakati pawo 
mwaubwino. Zimenezo 
Akulangizidwa nazo mwainu 
yemwe Akukhulupirira Mulungu 
Ndi tsiku lomaliza. Zimenezo 
nzabwino Kwa inu, ndiponso 
zoyeretsa. Ndipo Mulungu 
akudziwa, pomwe Inu simudziwa. 

233. Ndipo akazi omwe 
angobereka kumene Ayamwitse 
ana awo zaka ziwiri zathunthu 
Kwa yemwe akufuna kukwaniritsa 
kuyamwitsa. Ndi udindo wa 
abambo kuwapezera chakudya 
Chawo anawo ndi amayiwo, 
ndiponso Kuwapezera chovala 
chawo anawo ndi amayiwo, 
Motsatira malamulo a Shariya. 
Ndipo mzimu wa Munthu aliyense 
sukakamizidwa, koma m'mene 
Ungathere. Ndipo mayi 
wamwanayo asazunzidwe 



9' . \1'99 ^ul.j, 999* 9 \X 






1 Apa amuna akuwalangiza kuti awabwerere akazi awo mwachangu nthawi ya 
eda isanathe kuopa kuti ikatha ndiye kuti akwatiwa ndi amuna ena. Komatu 
akuwalangiza kuti abwererane nawo akaziwo ncholinga chokhala nawo 
mwaubwino, osati kubwererana nawo ncholinga chowavutitsa. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



76 



Y *>l 



Y SyM' ^J-** 



Chifukwa chamwana wakeyo. 
Nayenso bambo Wamwanayo 
asazunzike chifukwa chamwana 
Wakeyo. Ndipo lamuloli lilinso 
chimodzimodzi Pa mlowam'malo 
(ngati bambo atamwalira). Ndipo 
onse awiri ngati atafuna kumletsa 
Kuyamwa, mogwirizana Pakati pa 
awiriwo, ndimokambirana palibe 
Kulakwa pa iwo awiriwo. Ndipo 
Ngati mutafuna kuwapezera ana 
anu akazi Ena owayamwitsa 
(omwe si amayi awo), palibe 
Uchimo mwa inu ngati mwapereka 
chimene Mudalonjeza kuwapatsa 
(oyamwitsawo) Mwaubwino. 
Ndipo opani Mulungu; 
Dziwaninso kuti Mulungu akuona 
Zonse zimene mukuchita. 1 

234. Ndipo mwainu amene 
amwalira Nasiya akazi, choncho 



£$^^j&£a; 






^^i^^^lii^^ba^ 



1 Mwana amayamwitsidwa ndi mayi wake m'nthawi yazaka ziwiri. Ndipo 
akhoza kupitiriza kumuyamwitsa zitapita zaka ziwiri. Sikoletsedwa, koma 
sibwino. Ndipo mayiyo akhoza ngati atagwirizana ndi tate wamwanayo 
kumsiitsa zaka ziwiri zisanakwane ngati ali ndichitsimikizo choti mwanayo 
sapeza masautso. Ndipo tate ngati adalekana naye ukwati mayi wamwanayo 
pomwe mayiyo akupitiriza kuyamwitsa mwanayo, nkofunika kwa tate 
wamwanayo kupereka malipiro kwa mayi wamwanayo, monga kumpezera 
chakudya chake mayiyo ndi zovala zake ndi ndalama zolipirira pamalo 
pokhala ndi zina zotere. 

Mwamuna asanene kwa mkaziyo kuti "Uyu mwana wako. Tero uwona 
chochita naye." Pamenepo mpovuta chifukwa mkaziyo sangapeze munthu 
womthandiza iye ndi mwanayo. 

Makamaka izi zingachitike ngati mkaziyo sanakwatiwe ndi mwamuna wina. 
Nayenso mayi wamwanayo asamkhwimitsire mwamunayo malipiro operekedwawo. 
Koma zonse zikhale zaubwino. 

Ngati tate wamwanayo palibe, ndiye kuti mlowam'malo wa tateyo ndiye 
adzakwaniritse zimenezo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



77 



1 T»>i 



T S^aJi 5jj-*» 



(akaziwo) Ayembekezere 
(asakwatiwe) Miyezi inayi ndi 
masiku khumi. Ndipo akakwanitsa 
nyengo Ya chiyembekezero chawo 
cha Eda, sitchimo kwa inu 
Pazimene akaziwo adzichitira 
Okha (monga kudzikongoletsa Ndi 
kudziwonetsa kwa ofunsira 
Ukwati); komabe zikhale motsatira 
Mmalamulo a Shariya. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa zonse zimene 
mukuchita. 

235. Ndipo sitchimo kwa inu 
kupereka mawu Okuluwika 
ofunsira ukwati kwa akaziwo 
(Pamene chiyembekezero cha eda 
yawo Chisanathe. Ndiponso palibe 
uchimo) Kapena kubisa mumtima 
mwanu, Kuwakwatira 
(Chiyembekezo chawo 
Chikadzatha). Mulungu wadziwa 
kuti Mukhala mukuwakumbukira 
akaziwo. Koma Musawalonjeze 
mobisa (kuti: "Ikatha eda 
Ndidzakukwatira.)" Koma nenani 
mawu Abwino. Ndipo 
musatsimikize kumanga ukwati 
Mpaka nyengo yolembedwayo 
ikwanire. Ndipo Dziwani kuti 
Mulungu akudziwa zomwe zili 
M'mitima mwanu. Tero 
chenjeranayeni (Mulungu), 
dziwaninso kuti Mulungu 
Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza. 

236. Palibe tchimo pa inu 
mutawapatsa Akazi mawu 









£vty$&a$&'7&$ 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



78 



Y *>i 



Y 5jiJl 5jj-» 



achilekaniro pomwe 
Simudakhudzane nawo; pomwenso 
Simudawadziwitse gawo la 
chiwongo Chawo (mahari yawo); 
Koma asangalatseni powapatsa 
chilekaniro. Opeza bwino apereke 
malinga ndikupeza Bwino kwake; 
wochepekedwa apereke Malingana 
ndikuchepekedwa kwake. 
Chilekaniro chosangalatsacho 
chikhale Molingana ndi Malamulo 
a Shariya, Ndipo ndilamulo kwa 
Ochita zabwino. 1 

237. Ndipo ngati mwalekana 
nawo (akaziwo) Musanakhudzane 
nawo mutawadziwitsa Gawo 
lachiwongo chawo, apatseni Theka 
lachimene mudagwirizana 
Kuwapatsa pokhapokha ngati 
akaziwo atakana Okha (theka la 
chiwongocho), kapena 
(Mwamuna) uja yemwe 
kumangitsa kwaukwati Kuli 
m'manja mwake amusiire 
(chiwongo Chonsecho mkaziyo). 



1 Kuthetsa ukwati nkololedwa m'Chisilamu. Koma ngakhale nkololedwa 
Shariya ya Chisilamu imanyansidwa ndimachitidwe othetsa ukwati 
pokhapokha pakhale zifukwa zovomerezeka ndi Shariya. 
Ngati patapezeka zifukwa zochititsa kuti ukwati uthe nkofunika kuti mkwati 
amchitire mkwatibwi zabwino monga izi: 

a) ampatse chiwongo (mahali) chimene chinatsalira ngati sadamalize 
kupereka. 

b) ampatse ndalama zina zapadera zomtulutsira mkaziyo m'nyumba. 

c) ampatse chovala, malo okhala, chakudya patsiku lililonse kufikira eda yake 
itatha ngakhale edayo itatenga nthawi yaitali. 

d) amsiire zinthu zake kuti atenge pamodzi ndi zimene adampatsa. 
Nkosaloledwa kumlanda chilichonse mwazimenezi. 









Surat 2. AI-Baqarah Juzu 2 79 T *j*-i 



t S^flJl 3jj-a 



Ndipo ngati mutasiirana 
(Zimenezo) zingakuyandikitseni 
kumbali Yoopa Mulungu. Ndipo 
musaiwale kuchitirana Zabwino 
pakati panu (ngakhale kuti 
Mukulekana). Ndithudi Mulungu 
akuona zonse Zimene mukuchita. 1 

238. Sungani mokwanira Swala 
Makamaka Swala Yapakatikati; 
ndipo Imirirani modzichepetsa 
kwa Mulungu. 2 






1 Ngati udamkwatira mkazi ndipo nkulekana naye usanalowane naye, 
umpatse theka lachiwongo chomwe chidatchuiidwa. Ngati udampatsa 
chiwongo chonse, ndiye kuti akubwezere theka lake. Koma ndibwino kwa 
mwamuna kumpatsa mkazi chiwongo chonse ngati anali asanampatse. Ngati 
anampatsa asaitanitsenso chiwongocho. Ndibwinonso kwa mkazi kubweza 
chiwongo chonse ngati adampatsa chonse, kapena kukana kuti asampatse 
ngati anali asanapatsidwe. Aliyense mwa awiriwa asakhale ndi chibaba 
chofuna kupeza ndalama pakutha pa ukwatiwo. Malamulo tanenawa 
amagwira ntchito ngati chiwongo chidatchuiidwa kuchuluka kwake pomwe 
ankafunsira ukwati. Koma ngati chiwongocho sanachitchule kuchuluka kwake 
kotero kuti sadagwirizane za chiwongocho kuti adzapereka mwakutimwakuti, 
pamenepa ndiye kuti ampatse chinthu cholekanira choti chimsangalatse. Hi 
ndilo tanthauzo lazomwe zatchulidwa m'ndime ya 236. 

Ndithudi apa akutilangiza mwamphamvu kuti tizichitirana zabwino ngakhale 
panthawi yolekana ukwati. Anthu asaiwale ubwino ndi chikondi zomwe 
ankachitirana pakati pawo. 

2 M'ndime iyi akulimbikitsa kuti Swala zonse anthu azipemphere muunyinji 
wawo osati munthu payekhapayekha makamaka Swala yapakatikati. Ena 
mwa maulama adati Swala yapakatikati ndiswala ya Azuhuri. 
Imapempheredwa pakatikati pamasana, dzuwa litatentha kwambiri monga 
momwe zilili m'maiko a Arabu. 

Paswala ya Azuhuri anthu amavutika kwambiri kukapemphera m'misikiti 
chifukwa chakutentha kwa dzuwa. Choncho apa akuwalimbikitsa kuti 
azikapemphera m'misikiti ngakhale kuli kotentha. Pomwe ena akuti Swala 
yapakatikati ndi Swala ya Fajiri (Subuhi) imene imapempheredwa pakatikati 
panthawi. Simasana ndiponso siusiku. Apa mpanthawi pomwe tulo timakhala 
tamphamvu. Tero akuwalimbikitsa anthu kusiya tuloto nkupita kumisikiti 
nkukapemphera Swala ya (jama) yapagulu. Ndipo akutilimbikitsanso kuti 
tizipemphera mofatsira ndi modzichepetsa. Ndikuti tikamapemphera tizidziwa 
kuti taimirira pamaso pa Mulungu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



80 



r *>i 



T 0jiaJ\ 0jj~* 



239. Ndipo ngati muli ndi 
mantha (kupemphera Mwalamulo 
pamene mukumenyana Ndi adani 
anu), pempherani uku Mukuyenda, 
kapena mutakwera Chokwera. 
Ndipo mukakhala Pachitetezo 
mkumbukireni Mulungu 
(Pempherani) monga momwe 
Wakuphunzitsirani Zomwe 
simudali kuzidziwa. 

240. Ndipo mwainu amene 
amwalira nasiya akazi 
Awo,alangize (amlowam'malo 
awo) za akazi awo Kuti awapatse 
zodyera m'nyengo yachaka 
Chimodzi popanda kutulutsidwa 
(m'nyumba Zomwe ankakhala ndi 
amuna awo). Koma Ngati akazi wo 
atuluka (okha), palibe Kulakwa 
painu pazimene adzichitira okha 
Zomwe nzogwirizana ndi 
chilamulo cha Shariya. Ndipo 
Mulungu Ngwamphamvu Zoposa; 
Ngwanzeru zakuya. 

241. Ndipo akazi osiidwa 
ukwati, apatsidwe chilekaniro 
Chowasangalatsa m' chilamulo Cha 
Shariya. Hi ndi lamulo Kwa amene 
akuopa Mulungu. l 

242. Umu ndi momwe Mulungu 
Akukulongosolerani Ma aya 






' 99<*<. 









Pamene mwamuna akumsiya mkazi ukwati pafunika kuti ampatse chinthu 
china kuwonjezera pa chiwongo. Koma Asilamu ambiri kudera la kuno 
kum'mawa kwa Afrika m'malo mompatsa chinthu mkazi pomusiya amaitanitsa 
chinthu kwamkazi kuti awapatse kapena kumlanda katundu kumene. 
Machitidwe otere ngoipitsitsa, sali ogwirizana ndi malamulo a Chisilamu. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



81 



r *>» 



Y SyJ* ojj-» 



(ndime) Ake Kuti inu mukhale 
Ndinzeru. 

243. Kodi sudamve (nkhani za) 
amene adatuluka M'nyumba zawo 
ali zikwizikwi kuopa Imfa? Ndipo 
Mulungu adawauza: "Mwalirani", 
(ndipo adamwalira chabe Popanda 
chifukwa chilichonse). Kenako 
Adawaukitsa (kuti adziwe kuti 
imfa Njosathawika). Ndithudi, 
Mulungu Ndimwini kuchita 
zabwino pa anthu, koma Anthu 
ambiri sathokoza. l 

244. Ndipo menyani nkhondo 
panjira Ya Mulungu, ndipo 
dziwani Kuti Mulungu 
Ngwakumva, Ngodziwa 
chilichonse. 

245. Kodi ndani angamkongoze 
Mulungu Ngongole ya bwino 
(yochokera m'chuma Chake 
powapatsa amphawi ndi kupereka 
Pa njira ya Mulungu) kuti 
amuonjezere Zoonjezera zambiri? 
Ndipo Mulungu Ndi Yemwe 
amafumbata ndi Kutambasula, 
ndipo kwa lye Nkumene 
mudzabwezedwa. 2 









W&^^'dMl 









1 Ibun Abbas adati anthuwo adali zikwi zinayi. Adatuluka m'nyumba zawo 
kuthawa mliri wanthomba, nati pakati pawo: "Tipite kudziko lina komwe kulibe 
imfa yanthomba." Choncho adayenda mpaka kufika pamalo pena; ndipo 
Mulungu adati kwa iwo: "Mwalirani," ndipo onse anamwaliradi nthawi 
yomweyo. Ndipo mmodzi wa aneneri adawadutsa iwo ali akufa, nampempha 
Mbuye wake kuti awawukitse kuti azimgwadira. Choncho adawaukitsa. 
Nkhaniyi tikuphunziramo zoti imfa siithawika. 

2 Apa anthu akuwalimbikitsa kuti azipereka chuma chawo panjira zabwino 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



82 



T frjJt-1 



T SjiJl 5jj-a 



246. Kodi sudamve nkhani ya 
akuluakulu Aana a Israyeli 
pambuyo pa Musa? Adanena kwa 
mneneri wawo: "Tidzozere mfumu 
kuti timenye Nkhondo pa njira ya 
Mulungu." lye (Mneneri wawoyo) 
Adati: "Mwinatu simungamenye 
Nkhondoyo ngati kutalamulidwa 
kwa inu. (Iwo) adati: "Nchotani 
kuti tisamenye Nkhondo panjira ya 
Mulungu pomwe Tatulutsidwa 
m'nyumba zathu pamodzi ndi Ana 
athu?" Koma pamene 
adalamulidwa Kumenya 
nkhondoyo, adatembenuka, 
Kupatula ochepa mwaiwo. Ndipo 
Mulungu akudziwa Bwinobwino 
za anthu ochita zoipa. 

247. Ndipo Mneneri wawoyo 
adawauza: "Mulungu 
Wakusankhirani Taluti kukhala 
mfumu. (Iwo ) Adati: "Nchotani 
kuti iye akhale ndi ufumu Kuposa 
ife pomwe ife ngoyenera kupeza 
ufumu Kuposa iye, ndipo 
sadapatsidwe chuma Chambiri?" 
(Iye) adati: "Mulungu 
wamusankha Mwainu, ndipo 
wamuonjezera kukhala ndi Nzeru 
zopambana ndi kukhala ndi thupi 
(Lamphamvu). Ndipo Mulungu 
amampatsa Ufumu wake amene 
wamfuna. Ndipo Mulungu ndi 









ndipo Mulungu adzawalipira mphoto yambiri. Asachite umbombo kupereka 
chuma chawo m'njira zabwino pakuti sadaka siichepetsa chuma koma 
kuchichulukitsa. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



83 



y *>» 



T SjiJl 5j^i» 



Mwini zopereka zambiri, ndiponso 
Ngodziwa." 

248, Ndipo Mneneri wawo 
adawauza (kuti): "Chizindikiro 
chaufumu wake, Ndikukudzerani 
Bokosi lomwe mkati mwake Muli 
mpumulo wamiyoyo yanu 
wochokera Kwa Mbuye wanu, ndi 
zotsalira zomwe Adazisiya anthu a 
Musa ndi anthu a Haruna, 
Atalisenza Angelo. Ndithu, 
m'zimenezo muli Chisonyezo 
kwainu (chosonyeza kuyenera 
Kwa ufumu wake painu) ngati 
mulidi Okhulupirira." 

249. Choncho, Taluti pamene 
adapita ndi Magulu ake a nkhondo, 
adati: "Mulungu Akuyesani 
mayeso ndi mtsinje (womwe 
Mukumane nawo panjira komwe 
mukupitako). Choncho amene 
akamwe mmenemo sali nane. 
Koma amene sakamwa adzakhala 
pamodzi Nane kupatula amene 
watunga ndi dzanja lake 
(Ndikumwa; iyeyo ndiye kuti 
Sadalakwe). Koma (iwo) adamwa 
m'menemo Kupatula ochepa 
mwaiwo. Pamene adaoloka lye 
pamodzi ndi aja omwe 
adakhulupirira Limodzi naye, 
(Iwo) adati: "Lero Sitingamuthe 
Jaluti ndi magulu ake ankhondo." 
Ndipo omwe adali ndi chitsimikizo 
chokumana Ndi Mulungu adati: 
"Kodi ndimagulu angati Ochepa 



% 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 2 



84 



r *>i 



T S^aJi 5jj-* 



amene adagonjetsa magulu ambiri 
Mwachilolezo cha Mulungu! 
Ndipo Mulungu Ali pamodzi ndi 
opirira. 1 

250. Ndipo pamene adapita 
kukalimbana ndi Jaluti (mfumu ya 
adaniwo), pamodzi ndimagulu ake 
ankhondo (Anthu a Taluti) adati: 
"O! Mbuyewathu! Titsanulireni 
chipiriro, ndipo limbikitsani 
Mapazi athu; Tithangateni kwa 
Anthu osakhulupirira." 

251. Choncho, adawagonjetsa 
Mwachilolezo cha Mulungu. 
Ndipo Daud adapha Jaluti; Ndipo 
Mulungu adampatsa Ufumu ndi 
uneneri, namphunzitsanso Zimene 
adafuna. Mulungu akadapanda 
Kukankha anthu ena kupyolera 
Mwa anthu ena ndiye kuti dziko 
Likadaonongeka. Koma Mulungu 
Ndimwini kuchita zabwino 
Pazolengedwa zonse. 

252. Awa ndi ma aya (ndime) A 
Mulungu; tikuwawerenga kwa iwe 
(Mtumiki) Mwachoonadi. Ndithudi, 
iwe ndi we mmodzi mwa atumiki. 















1 Kumvera ndichinthu chachikulu kwabasi kuti zinthu za anthu ziyende bwino. 
Anthu osamvera zinthu zawo siziyenda bwino. Ndipo apa mfumuyi ikuchoka 
kupita kunkhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo lomwe lidali losamvera. 
Choncho Mulungu adaiuza mfumu ija kuti iwayese mayeso oti asamwe madzi 
othetsa ludzu lonse. Amene samvera asawatenge kunka nawo kubwalo 
lankhondo poona kuti angayambitse chisokonezo kumeneko. 

2 Mneneri Daud adali msirikali m'gulu lankhondo lamfumu Taluti. lye 
adamenya nkhondo ndi cholinga chabwino ndi mwaungwazi zedi mpaka 
adaipha mfumu ya adaniwo yomwe inkatchedwa Jaluti. Tsono Mulungu 
adampatsa ufumu chifukwa chakudzipereka kwakeko. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



85 



r *ji-i 



t O^flJl Ojj^t 



253. Amenewo ndi aneneri 
tidawapatsa ulemerero Mosiyanitsa 
pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa 
iwo alipo amene Mulungu 
adawalankhula; Ndipo ena 
adawakwezera kwambiri 
maulemerero Awo. Naye Yesu 
mwana wa Maria tidampatsa 
zisonyezo zooneka, ndi 
kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera 
(mngelo Gabriel). Mulungu 
akadafuna Sakadamenyana amene 
adalipo pambuyo pawo, (Pa 
atumikiwo) pambuyo powadzera 
Zizindikiro zooneka. Koma 
adasiyana. Choncho mwaiwo alipo 
amene adakhulupirira, Ndipo ena 
mwaiwo sadakhulupirire. Ndipo 
Mulungu akadafuna, 
Sakadamenyana; koma Mulungu 
Amachita zimene akufuna. ] 

254. E inu amene 
mwakhulupirira! Perekani mwa 
zimene takupatsani Lisanadze 



<£tfia«ag63ii<2& 

©43$* 






1 Ndime iyi ikusonyeza kuti Atumiki maulemerero awo ngosiyanasiyana kwa 
Mulungu monga momwenso alili anthu ndi Angelo ndi zinthu zinanso. 
Amaposana pakalandiridwe kaulemerero wawo kwa Mulungu chifukwa 
chakusiyana zochita zawo. Zochita za ena nzazikulu zedi kapena zochuluka 
kwambiri kuposa zochita za anzawo. Ndipo apa Mulungu watchulapo atatu 
mwa atumiki akuluakulu omwe ndi:- 

(a) Musa amene Mulungu adayankhula naye ndi kumpatsa zozizwitsa 
zoonekera. 

(b) Ndi mneneri Isa (Yesu) yemwe adampatsa ulemerero waukulu 

(c) ndi mneneri Muhammad (SAW). 

Enanso mwa Aneneri akuluakulu pali Mneneri Ibrahim ndi Mneneri Nuhi 
monga momwe ikufotokozera ndime ya chisanu ndi ziwiri (7) yam'surati 
Ahzabi. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



86 



r *>» 



t djiJl djj-- 



tsiku lomwe Lilibe kugula 
(chilichonse Chokupulumutsani) 
ngakhale Ubwenzi ngakhalenso 
chiombolo. Ndipo osakhulupirira 
Ndiwo anthu oipa. 

255. Mulungu palibe 
wopembedzedwa wina koma lye, 
Wamoyo Wamuyaya, Woimira ndi 
Woteteza chilichonse. Kusinza 
sikumgwira ngakhale tulo. Zonse 
zakumwamba ndi zapansi nza lye. 
Kodi ndani angathe kuombola 
Kwa lye popanda chilolezo 
Chake? Akudziwa zapatsogolo ndi 
zomwe zili pambuyo pawo ndipo 
zolengedwazo sizidziwa 
Chilichonse pa zomwe zili 
M'kudziwa Kwake kupatula 
chimene wafuna. Mpando wake 
wakwanira Kumwamba ndi pansi 
ndipo Sizimamvuta kuzisunga 
zimenezo. Ndipo lye (Yekha) 
Njemwe ali 

Wapamwambamwamba, 
Ngwamkulu kwabasi, 
(Ngolemekezeka kwambiri). 1 



«^#uJ$!^&$ 



sui- 1 






Ndime iyi ikutchedwa Ayat Kursii; ndime yolemekezeka kwambiri. Kwa 
Msilamu aliyense nkofunika kuizindikira bwinobwino ndimeyi kuti azindikire 
kuti palibe yemwe angamuike patsogoio kapena pambuyo koma lye Mulungu 
wapamwambamwamba. M'hadisi zambiri za Mtumiki akutilimbikitsa 
kuiwerenga ndimeyi m'malo awa:- 

a) tikatha kuchita salamu paswala iliyonse 

b) tisanagone 

c) pamene tikutuluka m'nyumba 

d) polowa m'nyumba 

e) tikadzazidwa ndimantha poopa chinthu chomwe tikuchiona ndi chomwe 
sitikuchiona 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 87 ? *>* 



T 5yiJl 3jj-j 



256. Palibe kukakamiza 
(munthu kulowa) M'chipembedzo; 
kulungama kwaonekera Poyera 
kusiyana ndi kusalungama. 
Choncho amene akumkana Satana 
nakhulupirira Mulungu, ndiye Kuti 
wagwira chigwiriro cholimba, 
Chomwe sichisweka. Ndipo 
Mulungu Ngwakumva; 
Ngodziwa. 

257. Mulungu ndi mtetezi wa 
amene Akhulupirira. 
Amawatulutsa kumdima 
Ndikuwalowetsa M'kuunika. 
Koma amene sadakhulupirire, 
Atetezi awo ndi asatana. 
Amawatulutsa m'kuunika ndi 
kuwalowetsa mumdima Iwo ndi 
anthu akumoto. M'menemo 
adzakhalamo muyaya. 

258. Kodi sudamve zayemwe 
adatsutsana ndi Ibrahim pa za 
Mbuye wake (Mulungu)? 
(Ankanyada) pachifukwa chakuti 
Mulungu adampatsa ufumu. 






> 









Arabu ena a muMzinda wa Madina, Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye) asanasamukireko adali kutsata chipembedzo cha Chiyuda. 
Koma ambiri aiwo adali kupembedza mafano. Pamene chidadza Chisilamu 
pafupifupi onse omwe ankapembedza mafano adalowa m' Chisilamu. Koma 
amene adali m'chipembedzo cha Chiyuda mpang'ono okha omwe adalowa 
m'Chisilamu. Ndipo ena ngakhale anali Arabu adatsalirabe m'chipembedzo 
cha Chiyuda. Choncho, atate omwe adali Asilamu pamodzi ndi abale ndi 
amuna awo adafuna kukakamiza mwamphamvu amene adali m'chipembedzo 
cha Chiyuda kuti alowe m'Chisilamu. Koma Mulungu adawaletsa kuti palibe 
kumkakamiza kuti alowe m'Chisilamu yemwe sakufuna. Munthu aliyense 
adapatsidwa nzeru yomzindikiritsa chabwino ndi choipa. Ngati afuna kusokera 
nkufuna kwake iye mwini. Ndipo Mulungu adzamulanga patsiku Lachimaliziro 
osati pano padziko lapansi. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



88 



r *>i 



T Oj^Jl Sjj-j 



Ibrahim adati: "Mbuye wanga ndi 
Yemwe Amapereka'moyo ndi 
imfa." lye adati: "Inenso 
ndimapereka moyo ndi imfa." 
Ibrahim Adati: "Mulungu 
amatulutsa dzuwa kuvuma, 
choncho iwe ulitulutse 
kuzambwe." Ndipo uja 
wosakhulupirira adangoti Kakasi, 
(kusowa chonena). Ndipo 
Mulungu Satsogolera anthu ochita 
zoipa. 1 

259. Kapena ngati fanizo la uja 
amene adadutsa Pafupi ndi mudzi 
umene madenga ndi zipupa zake 
zidaphwasuka (udaferatu) adati: 
"Kodi Mulungu adzaukitsa chotani 
mudzi uwu pambuyo pakufa 
kwake?" Ndipo Mulungu 
Adampatsa imfa kwanthawi 
yokwana zaka Zana limodzi (100), 
kenako adamuukitsa Namufunsa: 
"Kodi wakhala nyengo yotani?" 









M'nthawi ya Mneneri Ibrahim padali mfumu ina yodzikuza yomwe 
inkadzitcha kuti ndimulungu ndipo anthu ake adali kuipembedza. Pamene 
Mneneri Ibrahim adadza nayamba kuphunzitsa chipembedzo choona ndikuti 
iyeyo simulungu, mfumuyo idati kwa Mneneri Ibrahim: "Kodi Mulungu wako 
woonayo amachita chiyani?" lye adati "Amapereka moyo ndi kuperekanso 
imfa." Mfumuyo idachita ngati sidamvetse cholinga chamawu a Mneneri 
Ibrahim. Idati: "Nanenso ndimachita zimenezo. Taona mmene ndimachitira." 
Pompo adalamula kuti abwere nawo anthu awiri omwe adawalamula kuti 
aphedwe. lye adalamula kuti mmodzi aphedwe ndipo winayo amsiye. 
Choncho zidachitika. Tsono adamuuza Ibrahim: "Waona bwanji? Kodi wina 
sindidampatse moyo ndipo winayo imfa?" Mneneri Ibrahim pomwe anaona kuti 
mfumuyo ikungodzipusitsa daladala adaiuza chinthu chomwe iyo sikadatha 
kuchichita. Adati: "Mulungu amatulutsa dzuwa kuvuma ndipo iwe ulitulutse 
kuzambwe." Pamenepo mfumuyo idangoti kakasi, sidachite chilichonse 
ndiponso sidanene chilichonse. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



89 



r *>i 



X djA-Jl Ojj-rf 









Adati: "Ndakhala nthawi yatsiku 
limodzi, Kapena theka latsiku." 
(Mulungu) adati: "Koma wakhala 
zaka zana limodzi, ndipo ona 
Chakudya chako ndi zakumwa 
zako, sizinaonongeke 
(sizinavunde). Ndipo yang'ana 
Bulu wako (ali mafupa okhaokha 
oyoyoka);ndi Kuti ukhale 
chisonyezo kwa Anthu, 
(nchifukwa chake takuukitsa ku 
imfa). Ndipo yang'ana 
mafupa(abulu wako) momwe 
Tingawaukitsire, kenako 
nkumaaveka Minofu." choncho 
pamene zidazindikirika (kwa iye, 
woukitsidwayo), adati: 
"Ndikudziwa kuti Mulungu 
Ngokhoza chilichonse." 1 

260. Ndipo (kumbukira) pamene 
Ibrahim adati: "E! Mbuye wanga, 
ndionetseni mmene 
Mudzaaukitsire akufa." 
(Mulungu) adati: "Kodi 
sunakhulupirirebe?" Adati: "Iyayi, 
(Ndikukhulupirira), koma 
(ndikufuna kuona Zimenezo) kuti 
mtima wanga ukhazikike." 
(Mulungu) adati: "Choncho 
katenge mbalame Zinayi; 
uzisonkhanitse kwa iwe (mpaka 



Munthu ameneyu pamodzi ndi anzake panthawiyo sadali ndi chitsimikizo 
kuti Mulungu angaukitse munthu wakufa. Ankaganiza kuti nchinthu 
chosatheka kuchitika. Choncho Mulungu adamsonyeza zimenezo kupyolera 
mwaiye mwini kuti akauze anzake omwenso adali osakhulupirira zakuuka ku 
imfa. 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



90 



r *>i 



t o^aJi $JJ-» 



Uyizindikire mbalame iliyonse 
mmene ilili, Ndipo kenako 
uziduledule zonsezo 
Zidutswazidutswa ndikuzisakaniza 
ndi kuzigawa Mzigawo zinayi). 
Ndipo paphiri lililonse Ukaikepo 
gawo limodzi la zimenezo, ndipo 
Kenako uziitane. Zikudzera 
zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti 
Mulungu ndi Mwini mphamvu 
Zoposa, Ngwanzeru zakuya." 1 

261, Fanizo la amene akupereka 
chuma chawo Panjira ya Mulungu 
lili ngati fanizo Lanjere imodzi 
yomwe yatulutsa ngala Zisanu ndi 
ziwiri. Ndipo ngala iliyonse 
Nkukhalamo njere zana limodzi. 
Ndipo Mulungu amamuonjezera 
Amene wamfuna (kuposera 
pamenepa). Ndipo Mulungu ali 
Nazo zambiri, Ngodziwa. 



19 ">\ 99"\\'*'\ '9L m *9'9 *fi\<' 



Mneneri Ibrahim adalakalaka kuti aone mmene akufa adzaukira kuti 
chikhulupiriro chake chiwonjezeke mphamvu. Tero Mulungu adamulamula kuti 
azinge mbalame zinayi zosiyanasiyana mitundu. Kenako azisakanize ziwalo 
zake. Ziwalo za mbalame ina zilowe kumbalame ina. Tsono azigawe miyulu 
inayi.Mulu uliwonse akauike paphiri lakelake. Kenako aziitane mbalame zija. 
Ndipo aona kuti chiwalo chilichonse chikuthamangira kumbalame yake, 
pompo zonsezo zikhalanso mbalame zamoyo monga momwe zidalili 
poyamba. 

(Ndime 261-7) Ndime izi zonse zikulimbikitsa kupereka chuma panjira 
zabwino ndiponso zikuonetsa ubwino umene woperekayo amalandira kwa 
Mulungu. Komatu woperekayo kuti apeze ubwino wa Mulungu pafunika izi: 

(a) apereke chifukwa cha Mulungu osati ncholinga chodzionetsera kwa anthu, 

(b) choperekacho chikhale chabwino. Ngati wapereka zomwe sizabwino ndiye 
kuti sangapeze mphoto yaikulu, 

(c) asawakumbe amene akuwapatsawo. 

(d) Asawavutitse. Ndipo ngati atachita zimenezi ndiye kuti sangapeze 
mphoto koma kungotaya chuma pachabe. Kumbwezera mawu abwino 
wopempha nkopindulitsa kuposa sadaka yotonzera. 

(e) Chimene akuperekacho chikhale chaHalali (chololedwa). Osati chomwe 
adachipeza m'njira yosavomerezeka. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



91 



r *>i 



Y OjiJl djj^ 



262. (Anthu) amene akupereka 
chuma Chawo panjira ya Mulungu 
napanda Kutsatiza pazomwe 
aperekazo Kukumba, ndiponso 
masautso Iwo ali ndi mphoto kwa 
Mbuye Wawo ndipo pa iwo 
Sipadzakhala mantha; Ndiponso 
sadzadandaula. 

263. Mawu abwino, ndi 
kukhululukira (Amene 
wakulakwira) nzabwino zedi 
kuposa sadaka yotsatizidwa Ndi 
masautso. Ndipo Mulungu Ndi 
Yemwe ali wolemera kwambiri 
Ndiponso Woleza 
(Kwazolengedwa zake). 

264. E inu amene 
mwakhulupirira! Musaononge 
sadaka zanu pokumba Ndiponso 
popereka masautso, Monga yemwe 
akupereka chuma chake 
Modzionetsera kwa anthu, ndipo 
Sakhulupirira Mulungu ndi tsiku 
Lomaliza. Choncho fanizo lake lili 
ngati Thanthwe lomwe pamwamba 
pake pali dothi Kenako nkulifikira 
chimvula (nkuchotsa dothi Lonse 
lija), nkulisiya lopanda kanthu. 
Tero sadzatha kupeza chilichonse 
Pazimene adachita. Ndipo 
Mulungu satsogolera anthu 
osakhulupirira. 

265. Ndipo fanizo la anthu 
amene akupereka Chuma chawo 
chifukwa chofuna chiyanjo cha 












r^j&&\<&^Q.$\$&s 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



92 



r >>i 



Y SyM' <>jj-> 



Mulungu ndi kulimbikitsa mitima 
Yawo (pa chipembedzo cha 
Mulungu) lili ngati fanizo la 
munda umene uli Pachitunda, 
chiufikira chimvula tero 
Nubweretsa zinthu zake 
dzochuluka Moonjeza kawiri 
(kuposera pachikhalidwe Chake). 
Ndipo ngati chimvula 
sichidaudzere, Ndiye kuti 
yamawawa (nkuukwanira 
mundawo). Ndipo Mulungu 
akuona zonse zimene mukuchita. 

266. Kodi mmodzi wa inu 
angakonde Kukhala ndi munda 
wamitengo Yakanjedza ndi 
mphesa womwe Pansi pake 
mitsinje ikuyenda, iye Mmenemo 
napeza dzinthu 

dzamitundumitundu, numpeza 
ukalamba uku ali ndi ana ofooka; 
Ndipo kamvuluvulu wamoto 
naugwera (Mundawo), nupsereratu 
(Angazikonde Zimenezi)? umo 
ndimomwe Mulungu 
akukulongosolerani ma aya 
(Ndime za mawu ake) kuti 
muganizire. 

267. E! inu amene 
mwakhulupirira! Perekani zabwino 
zochokera M' zimene mwapeza ndi 
zimene Takutulutsirani m'nthaka, 
Ndipo musalinge kupereka Choipa 
chomwe inu simukadachilandira 
(Ngati akanakupatsani) 






J 









Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



93 



r *>i 



t djiJl 5jj-» 



pokhapokha Mochitsinzinira. 
(Nanga Mulungu Ndiye alandire 
choipacho)? Ndipo dziwani kuti 
Mulungu Ngolemera (ndiponso) 
Ngotamandidwa. 

268. Satana amakuopsezani ndi 
umphawi Ndikukulamulirani 
kuchita zoipa (Monga umbombo) 
pomwe Mulungu akukulonjezani 
chikhululuko Kuchokera kwa iye 
ndi ubwino (Waukulu ngati 
mupereka); ndipo Mulungu ali 
nazo Zambiri, Ngodziwa. 1 

269. Amapatsa nzeru 
(zothandiza) Amene wamfuna; 
Ndipo amene wapatsidwa Nzeru, 
ndithudi, wapatsidwa Zabwino 



® &4*6£&tglg£!fr3 









1 (Ndime 268-71) Apa Mulungu akuwalimbikitsa mtima amene akupereka kuti 

panthawi iliyonse pamene akupereka Mulungu adzawaonjezera. Ndipo 

akuwachenjeza kuti asamamvetsere udyerekezi wa Satana umene amauthira 

m'mitima yawo powauza kuti, "Ngati mupereka, musauka." Koma Mulungu 

akuwauza kuti, "perekani simusauka. M'malomwake mupeza bwino padziko 

lapansi ndi pa tsiku lomaliza." 

M'ndime zomwezi Mulungu wafotokoza za (lonjezo) "naziri" kuti naziri iliyonse 

imene tikumlonjeza Mulungu akuidziwa. 

Mawu oti "Naziri" nga Chiarabu. M'chichewa akuthandauza kuti, "ndikapeza 

chakuti ndidzachita chakutichakuti," "kapena kuti, akachira mbale wanga 

ndidzapereka chakutichakuti kwa Mulungu." 

Mawu anaziriwa siabwino pa malamulo a Chisilamu, ngakhale kuti anthu 

ambiri amakonda kuchita naziri poganizira kuti akatero Mulungu awayankha 

mwachangu namaganiziranso kuti naziri nchinthu chabwino m'Chisilamu 

pomwe chili chosafunika m'Chisilamu. 

Kusafunika kwa naziri m'Chisilamu kuli kotere: Umati, "Mulungu akandichitira 

chakutichakuti inenso ndichita chakutichakuti." Mawu oterewa sali mawu 

abwino ndiponso akusonyeza kupanda mwambo ndiponso akusonyeza 

umbombo. 

Chifukwa cha kuti munthu ofuna kupereka kanthu sanganene kuti "Muyambe 

mwandichitira chakuti ndipo ndikupatsani." Koma ngakhale zili choncho 

akwaniritsebe malonjezowo. Koma ngati malonjezowo ali pachinthu choletsedwa 

asawakwaniritse, ndipo m'malo mwake apereke dipo. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



94 



r frjA-i 



T S^aJi 5jj-» 






Wltf* 



zambiri. Ndipo (Zoterezi ) 
sakumbuka koma Eni nzeru okha. 

270. Ndipo chilichonse chomwe 
mungapereke Kapena naziri 
(lonjezo) iliyonse yomwe 
Mwalonjeza Mulungu, Ndithudi, 
Mulungu akudziwa Zonsezi. Ndipo 
anthu ochita Zoipa sadzakhala ndi 
athandizi. 

271. Ngati mupereka sadaka 
moonetsera, Ndibwino; Ngati 
mungaipereke mobisa, 
Ndikuipereka kwa osauka, 
umenewo Ndiubwino woposa kwa 
inu. Ndipo akufafanizirani zoipa 
Zanu (ngati mutero). Ndipo 
Mulungu Akudziwa nkhani zonse 
Za zimene mukuchita. 

272. Siudindo wako 
kuwaongola, koma Mulungu 
amamuongola amene Wamfuna, 
(udindo wako Nkulalikira kokha). 
Ndipo Chuma chilichonse chimene 
mungachipereke, (Phindu lake) lili 
painu eni, ndipo musapereke 
Pokhapokha pofunafuna chikondi 
cha Mulungu. Ndipo chuma 
chilichonse chimene 
Mungachipereke adzakubwezerani 
Mokwanira (mphoto yake), Ndipo 
simudzaponderezedwa. l 



1 Apa akumuuza Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) pamodzi ndi 
aliyense wolamula kuchita zabwino ndikuletsa kuchita zoipa kuti udindo wawo 
nkufikitsa uthengawo. Pa iwo palibe vuto ngati anthuwo savomereza, iwo 






9 1 9&' 9 *?> ' h9 l f *f < 






Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



95 



T tjfr\ 



t djijl 0jJ-*» 



273. (Sadakazo ziperekedwe) 
kwa amphawi amene 
Atsekerezedwa panjira ya 
Mulungu, amene Sangathe 
kuyenda padziko (Kukachita 
ntchito yopezera Zofunika pamoyo 
wawo). Amene Sadziwa za 
chikhalidwe chawo, 
Amawaganizira kuti ngolemera 
Chifukwa chakudziletsa kwawo 
(Kupemphapempha) . 
Ungawazindikire (Kuti 
ngosowedwa) ndi zizindikiro 
zawo. Sapempha anthu mwaliuma. 
Ndipo chabwino chilichonse 
chimene Mukupereka, ndithudi, 
Mulungu ali Wodziwa Zaicho. 

274. Amene akupereka chuma 
Chawo usiku ndi usana, Mobisa 
ndi moonekera, Ali ndi malipiro 
awo Kwa Mbuye wawo; Ndipo 
paiwo sipadzakhala Mantha, 
ndiponso sadzadandaula. 

275. Amene akudya riba 
(chuma cha katapira) Sadzauka 
(M'manda) koma monga Mom we 
amaimira munthu okhudzidwa Ndi 
ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi 
nchifukwa chakuti amanena: 
"Malonda ngolingana ndi 
katapira," pomwe Mulungu 
waloleza malonda ndipo waletsa 
Katapira. Ndipo amene wamufika 






9 9 '9 * 4 



A "A\ Sfl S S ' \9-l.M 






adzapezabe mphoto yolamulira zabwino ndikuletsa zoipa ngakhale kuti 
sanawatsatire. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



96 



r *jJi-i 



T 5yJl ojj^ 



ulaliki Wochokera kwa Mbuye 
wake (woletsa Katapira) nasiya, 
choncho chomwe Chidapita 
nchake. Ndipo chiweruzo chake 
Chili kwa Mulungu (akaona 
chochita naye). Koma amene 
abwerera (kuchita malonda 
Akatapira), amenewo ndiwo anthu 
akumoto, Mmenemo adzakhalamo 
muyaya. 



276. Mulungu amachotsa 
madalitso Pa (chuma cha) katapira 
Ndipo amaika madalitso 
Pachaulere. Ndipo Mulungu 
Sakonda aliyense 
Wosakhulupirira, wamachimo 
ambiri. 

277. Ndithudi, amene 
akhulupirira, nachita Zabwino, 
napemphera Swala moyenera Ndi 
kupereka chopereka (Zakati) Iwo 
akapeza malipiro Awo kwa Mbuye 
wawo. Ndipo pa iwo sipadzakhala 
Mantha ndiponso sadzadandaula. 

278. E! inu amene 
mwakhulupirira! Opani Mulungu, 
ndipo siyani Zimene zatsalira 
m'katapira, Ngati inu mulidi 
okhulupirira. 















1 Ndime iyi yikuletsa kukongoza m'njira yakatapira. Mulungu akumuopseza 
mwamphamvu munthu wodya riba. Akumuuza kuti adziwe kuti ali pankhondo 
yolimbana ndi Mulungu. Mulungu akukalipa zedi kwa anthu ochita malonda 
akatapira. Tero pewani kuchita malonda akatapira.. Kodi inu muli ndi nyonga 
zomenyerana ndi Mulungu? 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



97 



r *j*-i 



t djAJf $JJ-» 



279. Ngati simuchita 
(zimenezo), Dziwani kuti 
mukulimbana ndi Mulungu ndi 
Mtumiki Wake. Ndipo ngati 
mulapa, maziko Achuma chanu 
ndi anu. Musapondereze, ndiponso 
Musaponderezedwe. 

280. Ndipo ngati wokongola ali 
ndi mavuto, Choncho (wokongoza) 
amdikire mpaka Apeze bwino. 
Ngati inu (okongoza 
Mungakhululuke pakusiya 
Kuitanitsa ngongole) muisintha 
kuti Ikhale sadaka, ndibwino 
kwainu ngati Mukudziwa 
(zimenezo). 

281. Ndipo liopeni tsiku lomwe 
inu Mudzabwezedwa kwa 
Mulungu. Ndipo kenako munthu 
aliyense Adzalipidwa mokwanira 
pazonse Zimene adachita (Ndi 
manja ake), Ndipo iwo 
sadzaponderezedwa. 

282. E inu amene 
mwakhulupirira! 

Mukamakongozana Ngongole kwa 
nyengo yodziwika Ilembeni. Ndipo 
mlembi pakati Panu alembe 
mwachilungamo; Ndipo mlembi 
asakane kulemba Monga momwe 
Mulungu Wamphunzitsira; 
choncho alembe. Ndipo alakatule 
(mawu olembedwawo Ndi 
wokongolayo) yemwe ngongole ili 
paiye. Nayenso aope Mulungu, 












h&pm 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



98 



r >>» 



x SjiJi «jj-» 



Mbuye wake, ndipo asapungule 
Chilichonse M'menemo 
(m'ngongole). Ndipo ngati 
wokongola ndiozelezeka kapena 
Wofooka, kapena iye mwini 
sangathe Kulembetsa (Momveka), 
choncho amulembetsere 
Myang'aniri (Wakili) wake 
(yemwe Akuyang'anira zinthu 
zake) mwachilungamo. Ndipo 
funiraponi mboni ziwiri Zochokera 
mwa anthu anu aamuna (Asilamu). 
Koma ngati amuna awiri Palibe, 
choncho apezeke Mwamuna 
mmodzi ndi akazi awiri (Kuti 
aikire umboniwo), amene 
mumavomereza Kukhala mboni 
kuti ngati mmodzi mwaiwo (Akazi 
awiriwo) angaiwale Mmodzi 
wawo akumbutse winayo. Ndipo 
Mboni zisakane zikaitanidwa. 
Ndiponso Musanyozere kulemba 
(ngongoleyo) yaing'ono Kapena 
yaikulu mpaka nyengo yake. 
Zimenezo (Kulembako) ndibwino 
kwa Mulungu, ndipo 
Ncholungama zedi kumbali 
yaumboni, ndiponso Nchothandiza 
kuti musakhale ndi chipeneko. 
Koma akakhala malonda omwe ali 
Pompo omwe mukupatsana pakati 
panu (tsintho) Sikulakwa kwainu 
kusalemba. Koma Funani mboni 
pamene mukugulitsana. Komatu 
Asavutitsidwe mlembi ndiponso 
mboni. Ngati Mutachita zimenezo 






•r£ti-< 






Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



99 



Tf>l 



Y OjiJl Ojj-* 









(zoletsedwazo) kumeneko Ndiko 
kutuluka m'chilamulo cha 
Mulungu wanu, ndipo opani 
Mulungu, Mulungu 
akukuphunzitsani. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 1 

283. Ngati muli paulendo, ndipo 
Simudapeze mlembi, choncho 
(Wokongoza) apatsidwe chikole 
(Pinyolo) m'manja mwake. Ngati 
wina Wasungitsa mmodzi wainu 
chinthu (Omuyesa wokhulupirika) 
choncho Amene wayesedwa 
wokhulupirikayo Abweze 
chinthucho kwamwini wake, 
Ndipo aope Mulungu, Mbuye 
wake. Ndipo musabise umboni 
(Ngakhale uli wokuipirani). Ndipo 
Amene abise ndiye kuti mumtima 



1 Apa akuwalimbikitsa anthu kuti azilemba akamakongozana zinthu kuti 
pasakhale mkangano ndikukanirana kuti sanakongozane. Ngakhale 
ngongoleyo ikhale yochepa pafunika ndithu kulemba. Ndipo polembetsa 
ngongoleyo wokongolayo ndiye adzinena mawu olembedwawo poopa kuti 
akayankhula wokongoza akhoza kuonjeza mawu ndipo wokongola nkuchita 
manyazi kumbweza pakuti mkono wopempha ngwapansi pomwe wopereka 
ngwapamwamba. Ndipo pamene wolemba akuuzidwa kuti asawakanire 
kuwalembera osadziwa kulemba, akutanthauza kuti anthu azithandizana 
pakati pawo. Ndipo olemba akuwalangizanso kuti alembe zokhazo zomwe 
akuuzidwa ndipo afunirepo mboni zotsimikiza kuti alembadi. Ndipo mbonizo 
zisainire pamenepo. Oikira umboni afunika kukhala amuna awiri a Chisilamu. 
Ngati palibe amuna awiriwo, mmalo mwa mwamuna mmodzi zilowe mboni 
ziwiri za chikazi chifukwa chikumbumtima chaakazi nchochepa poyerekeza 
ndi chaamuna. Ndipo anthu akuwauzanso kuti akawapempha kuti aikire 
umboni pachinthu asakane. Kuikira umboni ndi ntchito yabwino yotsimikizira 
choona ndi kukana chonama. Koma pamalonda ogulitsana dzanja ndi dzanja 
sipafunika kulemba koma pamangofunika mboni basi. Ndipo pomwe 
kwanenedwa kuti "Asavutitsidwe olembawo ndi oikira umboniwo" akusonyeza 
kuti ngati ntchito yolembayo ndi kuikira umboniwo nzotenga nthawi yaitali 
kotero kuti olembawo ndi mbonizo iwachedwetsera ntchito zawo zomwe 
amapezera zowathandiza pamoyo wawo, ayenera kuwalipira. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 



100 



r *>i 



t 3jiJl 5jj-*» 



Mwake mwalowa utchimo; ndipo 
Mulungu akudziwa zonse zimene 
mukuchita. 1 

284. Zonse zakumwamba ndi 
Zapansi nza Mulungu. Kaya 
Muonetsera poyera zomwe Zili 
m'mitima mwanu kapena 
Kuzibisa, Mulungu adzakuchitirani 
Nazo chiwerengero. Kenako 
Adzakhululukira amene wamfuna 
(atalapa). Ndipo adzamlanga 
amene Wamfuna (akapanda 
kulapa). Ndipo Mulungu 
Ngokhoza chilichonse. 

285. Mtumiki wakhulupirira 
zimene zavumbulutsidwa Kwa iye 
kuchokera kwa Mbuye wake. 
Naonso Asilamu (akhulupirira). 
Onse Akhulupirira Mulungu, 
Angelo Ake, mabuku Ake ndi 
atumiki Ake. (I wo pamodzi ndi 
Mtumiki wawoyo akunena kuti): 
"Sitingalekanitse aliyense pakati 
pa atumiki Ake. (Onse 









1 Apa akunena kuti ngati anthu ali pamalo pomwe palibe wodziwa kulemba 
ndipo akukongozana, wokongozedwayo apereke chikole kwa wokongoza kuti 
achisunge wokongozayo. Ndipo adzabwezera akadzabweza ngongoleyo. 
Ngati atalephera kubweza ngongoleyo chikolecho chigulitsidwe ndi muweruzi 
nkumpatsa wokongozayo ndalama zolingana nzomwe adamkongoza. 
Zotsalira pachinthu chogulitsidwacho azipereke kwa mwini chikolecho. 
Uwu ndiwo ubwino wachikole pa Malamulo a Chisilamu. Akalephera kubweza 
ngongoleyo chinthucho chimagulitsidwa ndi Boma ndikumpatsa mwini 
ngongoleyo choyenerana naye pomwe chotsaliracho amachipereka kwa 
mwini wake. 

Kwa amene wagwirizira chikolecho saloledwa kuchita nacho chilichonse. 
Ngati akuchita nacho ntchito nkumachidyerera ndiye kuti akuchita machitidwe 
akatapira omwe ali oletsedwa. Koma chinthucho angochisunga. 



Siirat 2. Al-Baqarah Juzu 3 ioi T *jk-\ 



t SyLJl 5jj-*» 



tikuwakhulupirira)." Ndipo 
akunena: "Tamva ndiponso 
tamvera. (choncho 
Tikukupemphani) chikhululuko 
chanu, E! Mbuye Wathu! Ndipo 
kwa Inu nkobwerera." 1 

286. Mulungu sakakamiza 
mzimu Uliwonse koma chimene 
chili cholingana Ndi kukhoza 
kwake. (Ndipo phindu la) Zimene 
mzimuwo udapeza ndilake 
Ndiponso kuluza kwazomwe 
Udapeza nkwake. (Asilamuwo 






1 (Ndime 285-6) Ndime ziwirizi zili ndiubwino ndi madalitso ambiri monga 
momwe ilili ndime ya Ayatu Kursii yanambala 255 m'sura yomweyi. 
Akutilangiza kuziwerenga ndimezi m'malo monse momwe Ayatu Kursii 
imawerengedwa. Chimodzi mwazimenezo ndikuti iwo amavomereza atumiki 
onse a Mulungu amene adadza patsogolo pa Mneneri Muhammad (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye). Qur'an yonse ikuphunzitsa Asilamu kuti 
asasiyanitse pakati pa aneneri. Koma awavomereze onse ndi kuwakhulupirira 
amene adadza patsogolo pa Mtumiki Muhammad (SAW). Mtumiki 
Muhammad (SAW) ndiye womaliza mwa Aneneriwo. Ndipo amadziwika ndi 
dzina lakuti "Khatama nNabiyyina" "Womaliza mwa Aneneri." Ndipo amene 
sakhulupirira kuti Muhammad (SAW) ngomaliza mwa aneneri nakhulupirira 
munthu wamba yemwe akungodzinamiza kuti iye ndi mneneri, monga momwe 
chikhulupiriro cha Akadiyani chilili ndiye kuti iyeyo watuluka m'Chisilamu ndipo 
ndi munthu wakunja. 

Asilamu sakana mneneri aliyense mwa Aneneri omwe adalipo Mtumiki 
Muhammad (SAW) asanadze. Koma iwo amakhulupirira kuti malamulo 
akayendetsedwe kazipembedzo zawo kadafafanizidwa chifukwa chakudza 
kwa mtumiki Muhammad (SAW). Nyengo ino ndinyengo yotsatira mtumiki 
Muhammad (SAW) pazochitachita. Koma pazinthu zokhudza chikhulupiriro, 
Aneneri onse adadza ndi lamulo limodzi monga momwe Mulungu 
akufotokozera m'ndime ya 13, Surat Shura. 

Ndipo m'ndime zimenezi za 285 ndi 286 zikuphunzitsanso miyambo 
yaChisilamu ndi mapemphero (maduwa) momwe tingampemphere Mulungu. 
Ndimezi zikufotokoza za chisomo cha Mulungu chomwe chili pa ife anthu Ake 
kuti Mulungu sakakamiza koma chimene angathe kuchichita akapolo Ake. 
Ndiponso sawalanga ngati atachita zinthu molakwitsa kapena moiwala. 
Ndime ziwirizi zikusonyeza makhalidwe Asilamu ndi zinthu zawo zimene 
amazikhulupirira. 



Surat 2. Al-Baqarah Juzu 3 102 ? *> ( 



Y SyLJl ^JJ^ 



amanena) "O! Mbuye wathu! 
Musatilange tikaiwala Kapena 
tikalakwitsa, O, Mbuye wathu! 
Musatisenzetse mtolo 
(wamalamulo) monga 
munawasenzetsera amene adalipo 
Patsogolo pathu. O! Mbuye 
Wathu! Musatisenzetse chimene 
Sitingachithe. Tifafanizireni, 
tikhululukireni Machimo athu, 
ndiponso tichitireni chifundo. Inu 
Ndinu mtetezi wathu. Choncho 
Tithangateni ku anthu 
osakhulupirira." 







Siirat 3. Al-'Imran Juzu 3 



103 1" *>• T Wj** J T hf 




SURAT AL-'IMRAN III * 




Iyi ndi imodzi mwa Sura zomwe zidavumbulukira ku 
Madina, ndipo ndiimodzi mwasura zitalizitali. 

Surayi yafotokoza ngodya ziwiri zofunika m'chipembedzo 
cha Chisilamu zomwe ndi izi:- 

Ngodya yoyamba yafotokoza zachikhulupiriro ndi kupereka 
maumboni ndi zisonyezo zosonyeza umodzi wa Mulungu. Ngodya 
yachiwiri yafotokoza zamalamulo makamaka onena za kamenyedwe 
kankhondo yomenyera panjira ya Mulungu. 

Tsono m'tsatanetsatane wangodya yoyamba ija m'suramu 
mwadza mawu otsimikiza kuti Mulungu ndi mmodzi palibe 
wachiwiri kapena wachitatu. Ndipo alibe bambo, mwana kapena 
mkazi. Surayi yatsimikizanso kuti Mulungu adasankha anthu 
ena kuti akhale aneneri ncholinga choti afikitse kwa anthu 
uthenga wake. Ndipo yakambanso za choonadi cha Qur'an ndi 
kutsutsa zabodza zomwe anthu amachinamizira Chisilamu ndi 
Qur'an. Sura ya Bakara yafotokoza zambiri zachikhalidwe cha 
Ayuda ndi zolinga zawo zomwe nkukonda chiwembu ndi kuswa 
mapangano. Tsono sura ya Al-Imran yafotokoza za Akhirisitu 
omwe adatsutsana kwambiri ndi Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) pankhani yoti Yesu ndi mwana wa 
Mulungu kapena kuti ndi Mulungu amene pachifukwa choti 
anabadwa opanda tate. Ndipo iwo adatsutsanso uthenga wa 
Muhammad (SAW) ndi kumkana kuti simtumiki ndikutinso 
Qur'an sibuku la mawu a Mulungu. Surayi yakamba zaiwowa 
pafupifupi theka la surayi powayankha ndi kuwatsutsa pamawu 
awo omwe adali kukamba okhudza Mariya ndi Yesu popereka 
maumboni ndi zizindikiro zotsutsa kuti iwo sadali milungu. 

M'suramu mwakambidwanso nkhani za Ayuda pamodzi ndi 
kuwachenjeza Asilamu kuchiwembu chawo. Tsono 
patsatanetsatane wangodya yachiwiri, surayi yafotokoza ena 
mwa malamulo monga malamulo a Haji, Jihadi, zinthu zonena 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 104 T *>» 



T &j+* J^ 5jj-* 



za katapira (riba) ndi lamulo lonena za munthu wokaniza 
kupereka zakati. Mwakambidwanso m'suramu 

mwatsatanetsatane zankhondo, monga nkhondo ya Badri ndi 
Uhudi ndi maphunziro omwe Asilamu adatolamo m'nkhondozi. 
I wo adapambana pa nkhondo ya Badri nagonja pa nkhondo ya 
Uhudi, chifukwa chakusamvera kwawo langizo la Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye). Ndipo pambuyo 
pogonjetsedwa adatukwanidwa ndi Amunafikina ndi anthu 
osakhulupirira Mulungu. Kenako Mulungu anawafotokozeranso 
kuti cholinga cha Mulungu powalekerera Asilamu kuti agonje 
pankhondoyi, nkuti aonetsere poyera mwaiwo omwe adali 
ndichikhulupiriro champhamvu ndiomwe adali achinyengo. 

Surayi yafotokoza mwatsatanetsatane za amthirakuwiri omwe 
cholinga chawo chinali kudzetsa chisokonezo pakati pa 
Asilamu. Ndipo Surayi yamaliza nkulangiza anthu kuti alingarire 
za zolengedwa za Mulungu zakumwamba ndi zapansi zomwe 
zili zododometsa mkapangidwe kake kaluso zomwenso 
zikusonyeza kuti Mulungu Ngwamphamvu zoposa,Wopambana 
pachilichonse ndipo palibe chokanika kwa lye. 




Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 105 V *>» T 0\j** JT Sj^- 



SuratAl-'Imranlll 



:-"" 



%\..mm&;2:$:i 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1 . Alif-Lam-Mim} 

2. Mulungu (ndi mmodzi). 
Palibe winanso Wopembedzedwa 
mwa choonadi koma lye yekha, 
Wamoyo Wamuyaya, Woimira 



Ofr£\<£i$\&\j 



-^ 






Ndime makumi asanu ndi atatu zamsurayi zidavumbuluka chifukwa 
chanthumwi za Akhrisitu zochokera ku Najirani pamene zidadza kwa Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye). Nthumwizi zinali 60 okwera pa 
nyama.Mwa iwo mudali anthu khumi ndi anayi omwe adali olemekezeka awo. 
Ndipo atatu mwa iwo adali akuluakulu awo omwe ndi: Abdul Masihi, yemwe 
adali mtsogoleri wawo, Al-Ayihamu, yemwe adali mlangizi wawo, Abu Harisa 
bun Al-Kama, yemwe adali wansembe wawo. Pamene adakumana ndi 
Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) atatu aja mwa iwo ndiwo 
adalankhula nati: "Yesu 1 ndiye Mulungu chifukwa chakuti iye adali kuutsa 
maliro." Penanso adati: "lye ndi mwana wa Mulungu chifukwa choti inu 
simukudziwa kuti Mbuye wathu Mulungu ngwamoyo wamuyaya, safa, pomwe 
adalibe bambo." Natinso: "lye ndi mmodzi mwa atatu chifukwa chakuti 
Mulungu adati, "tidachita," 

"tidati." Akadakhala mmodzi akadati "Ndidachita; ndidanena." Mtumiki 
Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adati kwaiwo: "Kodi Yesu 
ngwakufa?" Iwo adati: "Inde." Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
adatinso: "Kodi simukudziwa kuti sipangakhale mwana pokhapokhapo 
atafanana nditate wake?" Iwo adati: "Inde." lye adatinso: "Kodi simukudziwa 
kuti Mbuye wathu Mulungu ndiYemwe akuimiririra chinthu chilichonse 
pochisunga ndi kuchipatsa zofuna zake? Kodi Yesu amachita chilichonse 
mwazimenezi?" Iwo adati: "lyayi" Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale 
naye) adatinso: "Kodi simukudziwa kuti kwa Mulungu palibe chingabisike 
chakumwamba ndi chapansi? Nanga Yesu amadziwa chilichonse mwazimenezo 
osati chokhacho chimene wadziwitsidwa?" Iwo adati: "lyayi." Ndipo iye 
adatinso: "Kodi simukudziwa kuti Mbuye wathu Mulungu sakudya chakudya 
ndipo sakumwa ndiponso sadzithandiza pomwe Yesu adali kudya ndi kumwa 
ndipo adali kudzithandiza?" Iwo adati: "Inde." Ndipo Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) adati: "Nanga iye angakhale bwanji Mulungu monga 
momwe mukunenera?" Onse adangoti kakasi. Komabe adapitiriza kumkana 
Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye). Choncho 
Mulungu chifukwa cha iwo adavumbulutsa ndime zam'surayi kuyambira 
ndime 1 mpaka 80. 



Surat 3. Al- 4 Imran Juzu 3 



106 



r *j*-i 



T Olj^P JT 5jj-* 



Ndi kuteteza chilichonse. 

3. Wakuvumbulutsira Buku 
Mwachoonadi, lomwe 
Likutsimikizira zomwe Zidalipo 
patsogolo pake. Ndipo 
adavumbulutsa Taurat ndi Injili - 
(Chipangano Chatsopano). 

4. Kale, kuti (mabukuwo) 
akhale chotsogolera Anthu. 
Ndipo adavumbulutsa (Qur'an) 
Cholekanitsa pakati pa choonadi 
ndi chonama. 2 Ndithudi, aja 
amene sadakhulupirire zizindikiro 
za Mulungu, adzakhala ndi 
chilango chaukali. Ndipo 
Mulungu ngwamphamvu 
Zoposa, wobwezera (Chilango 
mwaukali). 

5. Ndithudi, kwa Mulungu 
Sikungabisike chilichonse 
Chapansi ngakhale chakumwamba. 

6. lye ndi Yemwe 
amakulinganizani Muli m'mimba 
mmaonekedwe Anu mmene 












Mulungu ndiyekhayo woti nkumpembedza. Palibe wina wompembedza 
mwachoonadi koma lye basi. Padziko lonse lapansi ndi kumwamba palibe mwini 
mphamvu zoposa wogonjetsa chilichonse koma lye yekha basi. lye ndi Yemwe 
amadzetsa zabwino ndikubweretsa zoipa, osati wina aliyense. lye Ngwamoyo 
Wamuyaya, moyo wopanda chiyambi ndiponso wopanda malekezero. lye 
Ngwachikhalire kuyendetsa zinthu zazolengedwa zake. Thambo ndi nthaka 
adazikhazikitsa. Apa nkuti Mneneri Yesu asanamlenge. Choncho, Yesu sali 
Mulungu koma ndimmodzi wa aneneri. 

2 Tanthauzo la ndime iyi nkuti yakuvumbulukira iwe Muhammad (SAW) iyi 
Qur'an mwachoonadi popanda chipeneko kuti idachokera kwa Mulungu. 
Yatsika kupyolera mkudziwa Kwake itsimikizire zimene ztdali m'mabuku 
apatsogolo pake. Ndipo pazimenezi angelo ndimboni. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



107 r *>» 



V OIj^p JT 3jj-- 



akufunira. Palibe wopembezedwa 
Mwachoonadi koma lye; 
Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 

7. lye ndiYemwe 
wakuvumbulutsira Buku (ili la 
Qur'an), lomwe mkati Mwake 
muli ndime zomveka zomwe Ndi 
maziko a Bukuli. Ndipo Zilipo 
zina zokuluwika. Koma amene 
M'mitima mwawo muli kusokera, 
Akutsata zomwe zili zokuluwika 
Ndi cholinga chofuna kusokoneza 
Anthu, ndikufuna kudziwa 
tanthauzo Lake lenileni, Palibe 
amene akudziwa Tanthauzo lake 
lenileni koma Mulungu basi. 
Koma Amene azama 
pamaphunziro, amanena: 
"Tawakhulupirira (ma aya 
amenewa). Onse Ngochokera kwa 
Mbuye wathu," Ndipo palibe 
angakumbukire Koma eni nzeru 
basi. 

8. (Anzeruwo amanena): " O! 
Mbuye wathu! Musaikhotetse 
mitima Yathu pambuyo 
potiongola. Tipatseni chifundo 
chochokera Kwa Inu. Ndithudi, 
Inu Ndinu wopatsa kwambiri. 

9. O! Mbuye wathu! Inu ndinu 
Wosonkhanitsa anthu patsiku 
Lopanda chikaiko, Ndithudi, 
Mulungu Saswa lonjezo. 









I) 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



108 



r *>i 



T OI^aP JT 5jj-*» 



10. Ndithu, amene 
sadakhulupirire, Chuma chawo 
sichidzawathandiza Chilichonse 
ngakhalenso Ana awo, kuchilango 
cha Mulungu. Ndipo iwo Ndi 
nkhuni zakumoto. 

11. (Khalidwe la awa 
osakhulupirira, amumbadwo Wako 
iwe Mneneri Muhammad {SAW}, 
liri) Ngati khalidwe la anthu a 
Farawo ndi amene Adalipo 
pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa 
Zisonyezo zathu. Choncho, 
Mulungu Adawakhaulitsa 
chifukwa cha machimo awo. 
Ndipo Mulungu Ngolanga 
mwaukali. 

12. Auze amene 
sadakhulupirire: "Posachedwapa 
mugonjetsedwa 
Ndikusonkhanitsidwa 
ndikuponyedwa Kumoto. Taonani 
kuipa kwa Malo wokhazikika." 1 



^ 9 









Mawu adalandiridwa kuchokera kwa Said bun Jubeir omwe iye 
adawalandiranso kuchokera kwa Ikirama pomwe nayenso Ikirama adawalandira 
kuchokera kwa Ibinu Abbas (Mulungu asangalale nawo onse). lye adati: 
"Ndithudi, Mtumikl (madalitso ndi mtendere zikhale naye) pamene 
adagonjetsa Akuraishi pankhondo ya Badri nabwerera ku Madina 
adawasonkhanitsa Ayuda mumsika wa Bani Kainuka nawachenjeza kuti 
chingawapeze chomwe chidawapeza Akuraishi. Iwo adati: "Usanyengedwe 
ndizimenezo. 

Ndithudi, iwe unakumana ndi mbuli za anthu zomwe sizidziwa kamenyedwe 
kankhondo. Ndipo nchifukwa chake wawagonjetsa. Ukadamenyana ndi ife 
ukadadziwa kuti ife ndife anthu." 

Pachifukwa ichi idavumbulutsidwa aya (ndime) yakuti: "Nena (kwa iwo iwe 
Muhammad {SAW}): "Inu Ayuda mugonjetsedwa posachedwapa pompano 
padziko lapansi. Chuma chanu ndi ana anu zisakunyengeni. Kupambana 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 109 T *>» 



T OIj^p JT djj^t 



13. "Ndithudi, padapezeka 
chisonyezo chachikulu Kwa inu 
m'magulu awiri omwe adakumana 
(Tsiku lankhondo ya Badri), 
pomwe gulu Limodzi limamenya 
(nkhondo) panjira ya Mulungu, 
pamene linalo lokanira (ndipo 
gululo) Linkawaona (Asilamu) 
kukhala ochuluka kawiri Kuposa 
ilo, poona ndi maso awo. Ndipo 
Mulungu amamlimbikitsira 
mphamvu Ndi chipulumutso chake 
amene wamfuna. Ndithudi, 
m'zimenezo muli malingaliro 
(akulu) Kwa eni kupenyetsetsa 
mwanzeru." 

14. Kwakometsedwa kwa anthu 
kukonda Zilakolako (Zamoyo 
monga) akazi, ana, Milumilu 
yachuma cha golide ndi Siliva ndi 
mahachi oyang'aniridwa Bwino, 
ziweto, ndi mbewu. Izo ndi 
zosangalatsa za moyo Wadziko 
lapansi (zomwe sizilikanthu). 
Koma kwa Mulungu ndiko kuli 
Mabwerero abwino. 

15. Nena: "Kodi ndikuuzeni 
zomwe Zili zabwino kuposa 
zimenezo? Kwa omwe ali olungama, 
Akapeza kwa Mbuye wawo Minda 
yomwe pansi Pake ndi patsogolo 









KsJ6 9 9 9% *\' } *' * 9 



sikuli pachifukwa chakuchuluka kwanu, koma kuli m'manja mwa Mulungu 

Woyera." 

Mawuwa adatsimikizika powapha a Bani Nazwiri ndi kugonjetsa mzinda wa 

Khaibar. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 110 ? *> ( 



T OIj^p JT djy* 



pake Mitsinje ikuyenda; 
Adzakhala Mmenemo muyaya 
ndikulandira Akazi oyeretsedwa 
ndi chiyanjo Chochokera kwa 
Mulungu. Ndipo Mulungu akuona 
Akapolo ake onse. 

16. Omwe akunena: "Mbuye 
wathu! Ndithudi, ife takhulupirira. 
Choncho tikhululukireni Machimo 
athu ndikutipewetsa Kuchilango 
chamoto." 

17. Opirira onena zoona, 
omvera, Opereka chaulere ndi 
Opempha chikhululuko Nthawi 
yam ' bandakucha. 

18. Mulungu (mwini) akuikira 
umboni kuti: "Palibe 
wopembedzedwa mwachoonadi 
koma lye basi." Ndipo akuikiranso 
umboni (Zomwezi) angelo ndi eni 
nzeru (kuti lye) Ngokhazikitsa 
chilungamo. Palibe wina 
Wopembedzedwa mwachoonadi 
koma lye. Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 

19. Ndithudi, chipembedzo 
(choona) kwa Mulungu ndi 
Chisilamu. Ndipo amene 
Adapatsidwa Buku (Ayuda ndi 
Akhrisitu) sadatsutsane koma 
pambuyo Powabwerera 
kuzindikira. (Adatsutsana) 
Chifukwa chadumbo lomwe lidali 
Pakati pawo. Ndipo amene 



M 












&&&£m 






Surat 3. AI- 4 Imran Juzu 3 



111 



r*>» 



T OIj*p JT $jj*t 



akukana Zisonyezo za Mulungu, 
(Mulungu akamulanga pa tsiku 
lachiweruzo). Ndithu Mulungu 
Ngwachangu powerengera. 

20. Ngati (osakhulupirira) 
atsutsana nawe, Nena: 
"Ndayang'anitsa nkhope yanga 
Kwa Mulungu (ndadzipereka kwa 
lye) Pamodzi ndi amene 
anditsata." Ndipo Nena kwa onse 
adapatsidwa Buku (Ayuda Ndi 
Akhrisitu) ndi osadziwa kulemba 
Ndi kuwerenga (Arabu): "Kodi 
mwagonjera (Kwa Mulungu)?" 
Ngati agonjera ndiye Kuti 
aongoka: Koma ngati 
atembenukira Kumbali, udindo 
wako ndikufikitsa uthenga Basi. 
Ndipo Mulungu akuona akapolo 
ake onse. 

21. Ndithudi, amene akutsutsa 
Zizindikiro za Mulungu ndikupha 
Aneneri popanda choonadi 
Ndikuphanso anthu omwe 
Akulamula (kuchita) zolungama, 
Auze nkhani ya chilango 
chopweteka. 

22. Iwowo ndi omwe zochita 
Zawo zaonongeka Padziko lapansi 
ndi patsiku Lomaliza. Ndipo iwo 
sadzapeza athandizi. 

23. Kodi sukuwaona omwe 
apatsidwa Gawo la Buku (la 
Mulungu)? Akuitanidwa ku Buku 









^\$^m&$\'dm 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



112 



r *>i 



T b\y>* JT 5jj-*» 









la Mulungu Kuti liwaweruze 
pakati pawo; Kenako gulu Una la 
iwo Likutembenukira kumbali iwo 
ali onyoza. 

24. Zimenezo (kusalabadira 
malamulo a Mulungu) Nchifukwa 
chakuti amanena: "Sudzatikhudza 
Moto koma masiku ochepa basi". 
Ndipo Zawanyenga 
pachipembedzo chawo zomwe 
Adali kupeka (kuti 
adzakhululukidwa kapena 
Kulangidwa masiku ochepa okha). 

25. Kodi zidzakhala zotani 
pamene Tidzawasonkhanitsa tsiku 
lopanda Chikaiko? Ndipo mzimu 
uliwonse Udzalipidwa mokwanira 
pa Zomwe udachita. Ndipo iwo 
Sadzaponderezedwa. 

26. Nena "O! Mbuye wanga! 
Mwini Ufumu wonse. 
Mumapereka ufumu kwa yemwe 
mwamfuna. Ndipo Mumachotsa 
ufumu kwa yemwe Mwamfuna. 
Mumapereka ulemerero Kwa 
emwe mwamfuna, ndipo 
Mumamsambula yemwenso 
mwamfuna. Ubwino wonse uli 

1 Ndimeyi anthu omasulira Qur'an akuti ikufotokoza nkhani za Ayuda pamene 
adadza kwa Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) mmodzi mwaiwo 
atachita chiwerewere kuti arrive chilamulo chawochita chiwerewere. Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) anagamula kuti amulase ndi miyala 
mpaka afe. Koma iwo anakana. Anati; "M'Buku lathu mulibe chilamulo 
chotere." Ndipo adawauza kuti abwere nalo bukulo. Atabwera nalo anapeza 
kuti chilamulocho chilipo. Ndipo anawalasa miyala. Zitachitika tero, Ayuda 
anakwiya. 






>&&m6$^m&\$ 



fi:?'^^^ 



9 >." 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



113 



T *jir\ 



T Jtj^P JT $jj-- 



m'manja mwanu. Ndithudi, Inu 
ndinu Wokhoza chirichonse. 

27. "(Inu) mumalowetsa usiku 
muusana (Ndikukhala usana 
wautali monga m'nyengo 
Yotentha). Ndipo Mumalowetsa 
usana muusiku (Nkukhala usiku 
wautali monga m'nyengo 
Yachisanu). Mumatulutsa cha 
moyo M'chakufa; Ndipo 
mumatulutsa chakufa 
M'chamoyo. Ndipo mumapatsa 
Riziki (Chakudya) amene 
mwamfuna Mopanda 
chiwerengero." 1 

28. Asilamu asapale ubwenzi 
osakhulupirira Kusiya Asilamu 
anzawo. Amene Achite zimenezo, 
sadzakhala ndi Chilichonse 
pachipembedzo cha Mulungu, 
kupatula (kupalana Nawo ubwenzi 
mwachiphamaso) Chifukwa 
chakudzitchinjiriza kwa iwo. 
Ndipo Mulungu lye mwini 
Akukuchenjezani (za chilango 
chake). Ndipo kobwerera ndi Kwa 
Mulungu (basi). 

29. Nena: "Ngati mubisa 
zomwe Zili m'zifuwa zanu, kapena 
Kuzionetsa (poyera), Mulungu 
Akuzidziwa. lye akudziwa Zonse 












1 M'njere mumatuluka mmera. Ndipo njere imatuluka mummera. Dzira limatuluka 
m'nkhuku, ndipo nkhuku imatuluka m'dzira. Wosakhulupirira amabereka 
wokhulupirira. Ndipo wokhulupirira amabereka wosakhulupirira. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 114 T *>i 



T OIj*p JT 5jj-i 






hW-* 



&&&&&&(&&$& 



©;*-?->->- 



*&&\$t&$ȣ 



zakumwamba Ndi zapansi. Ndipo 
Mulungu Ngokhoza chilichonse." 

30. "Tsiku lomwe mzimu 
uliwonse Udzapeza zabwino 
zomwe Udachita zitabweretsedwa, 
Ndiponso zoipa zomwe udachita; 
Udzalakalaka kuti pakadakhala 
Mtunda wautali pakati 
Pamachimo ake ndi iye. Ndipo 
Mulungu Mwini Akukuchenjezani 
za chilango Chake. Ndipo 
Mulungu ngoleza Kwa akapolo 
ake. 1 

31. Nena: (iwe Mtumiki) "Ngati 
inu Mukumkonda Mulungu, tsatani 
ine; Mulungu akukondani 
Ndikukukhululukirani machimo 
Anu. Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka, Ngwachisoni." 2 

32. Nena: "Mverani Mulungu 
ndi Mtumiki (wake)". Koma ngati 
Akana, (Mulungu Awakhaulitsa). 
Ndithudi, Mulungu sakonda Anthu 
osakhulupirira. 

33. Ndithudi Mulungu 
adasankha Adam ndi Nuh ndi 
banja La Ibrahim ndi banja la Imran 
pa zolengedwa Zonse (anthu onse). 

1 Tsiku lachimaliziro (kiyama) munthu adzalakalaka kuti asawaone machimo 
ake amene adachita. Koma kuti machimowo akhale kutali ndi iye pomwe 
machimowo akamawachita amakhala wosangalala. 

2 Kungonena chabe pakamwa kuti ndikumkonda Mtumiki Muhammad (SAW) 
pomwe zochita zako nzosalingana ndimalangizo a Mtumiki Muhammad 
(SAW), chikondi chotere chilibe phindu lamtundu uliwonse. Ngati Muhammad 
(SAW) tikumkondadi timumvere ndi Kumuyesa chitsanzo chathu pazochita 
zathu zonse. 









Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



115 



r *>i 



T OIjaP JT ojj-i 






34. Ana; ena kuchokera Mwa 
ena pakati pawo. Ndipo Mulungu 
Ngwakum va, Ngodziwa. l 

35. (Kumbukirani) pamene 
adanena Mkazi wa Imran (Mayi 
wa Mariam (Maria), 
M'mapemphero ake): "Mbuye 
wanga! Ndapereka Kwa inu 
chimene chili m'mimba Mwanga 
monga "Wakfu" (wotumikira 
M'kachisi Wanu). Tero landirani 
Ichi kwa ine. Ndithudi, Inu Ndinu 
Akumva, Wodziwa. 2 

36. Choncho pamene adam'bala 
adati: "Mbuye wanga! Ndabala 
wamkazi!" Ndipo Mulungu 
akudziwa kwambiri Chimene 
wabereka - "Ndipo Wamwamuna 
(yemwe ndimayembekezera 
Kubala) sali ngati wachikazi 
(amene Ndamubala. Sangathe 
kutumikira Moyenera mkachisi 
wanu). Ndipo ine ndamutcha 
Mariam (Wotumikira Mulungu). 

1 Ndime iyi ikusonyeza kuti mawere awa ali olumikizana. Ndipo ikusonyeza 
kuti anthu abwino ambiri amabala anthu abwino. Tero amene akufuna 
kukwatira asankhe nyumba yabwino yachipembedzo, yamaphunziro ndi 
yaluso. 

2 (Ndime 35-6) Mkazi wa Imran pamene adali ndi pakati, ankaganiza kuti 
adzabereka mwana wa mwamuna. Ndipo adalonjeza kwa Mulungu kuti 
mwanayo adzampereka kuti akhale wotumikira ku Msikiti wa Baiti Limakadasi 
(Yelusalemu), ndi kutinso adzatumikire pazinthu zina zachipembedzo. Ntchito 
yake idzangokhala yokhayo. Koma mwatsoka adabereka mwana wamkazi 
ndipo kuti adzakhale mwana wabwino nkutinso adzabereke ana abwino. 
Adamutcha otumikira Mulungu. Tero mayi Mariam adali mayi wabwino. Ndipo 
nayenso adabala mwana wabwino yemwe ndi Mneneri Isa (Yesu). Mariam ndi 
mayi wolemekezeka kwabasi. 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



116 r *>» 



T ti\y>* JT 5jj-- 



Ndipo ndikupempha Chitetezo 
Chanu Pa iye ndi ana ake kwa 
Satana wothamangitsidwayo". 

37. Choncho Mbuye wake 
adamulandira, Kulandira 
kwabwino; namkulitsa, Kukulitsa 
kwabwino. Adampatsa Zakariya 
kuti amulere. Nthawi Iliyonse 
Zakariya akamulowera Mchipinda 
mwake (mwa Mariam) 
M'kachisimo, amampeza Ali ndi 
chakudya. Amati; "I we, Mariam! 
ukuzipeza kuti izi?" (Iye) amati: 
"Izi zikuchokera kwa Mulungu. 
Ndipo Mulungu Amampatsa 
yemwe wamfuna popanda 
Chiyembekezo (mwini wakeyo)". 1 

38. Pompo Zakariya adapempha 
Mbuye wake Nati: "Mbuye wanga! 
Ndipatseni Kuchokera kwa Inu 
mwana wabwino. Ndithudi, Inu 
ndinu Akumva pempho!" 

39. Mwadzidzidzi, mngelo 
adamuitana Uku iye ataimirira 



HWA'Zite. -r A»i>['&'S'JSZz 









Bambo Imran, tate wake wa Mariam, adali munthu wamkulu mwaanthu 
akuluakulu owopa Chauta panthawiyo. Atamubala mwana wakeyu iye 
adamwalira. Choncho akuluakulu amene adali naye pamodzi, anapikisana 
pankhani yolera Mariam. Kenako adagwirizana kuti achite mayere. Amene 
amgwere ndiyemwe alere Mariam. Tero mayerewo adakomera Mneneri Zakariya, 
mwamuna wa mayi wake wamng'ono wa mariam. Ndipo Mulungu adamsonyeza 
Zakariya zododometsa zambiri kwa mwanayo. Zina mwazododometsa ndiko 
kupeza chakudya pamalo pomwe ankakhala mwanayo chomwe chidali 
chosadziwika kwa anthu kumene chachokera. Ndipo akamufunsa amati Mulungu 
ndiye wampatsa. 

2 Mneneri Zakariya ataona zododometsazo, adaganiza kuti nayenso 
apemphe kuti amninkhe chozizwitsa chobala mwana pomwe adali wokalamba 
zedi. Nayenso mkazi wake adali chumba. Ndipo adamubaladi mneneri 
Yahaya (Yohane). 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



117 



r *>» 



T OIj^p JT hjj^t 



akupemphera Mchipinda cha 
m'kachisi: "Mulungu akukuuza 
nkhani yabwino (Yakuti ubereka 
mwana; dzina lake) Yahaya 
yemwe adzakhala wotsimikizira 
(Mneneri yemwe adzabadwa) ndi 
liwu Lochokera kwa Mulungu, 
(yemwe ndi Mneneri Yesu) amene 
adzakhalanso wolemekezeka ndi 
Wolungama ndi mneneri wa mwa 
anthu abwino. 

40. (Zakariya) adati: "Mbuye 
wanga! Ndidzakhala bwanji ndi 
mwana Pomwe ukalamba 
wandifikira, Nayenso mkazi wanga 
nchumba" (Mngelo adati) 
"Ndimomwemo; Mulungu 
amachita Chimene wafuna." 

41. (lye) adati: "Mbuye wanga! 
Ndipatseni Chizindikiro!" Adati: 
"Chizindikiro chako Ndikuti 
sudzatha kulankhula ndi anthu 
mpaka Masiku atatu koma 
momangolozera (ndi Chala) basi. 
Ndipo tamanda Mbuye wako, 
Kutamanda kwambiri ndiponso 
Umlemekeze (popemphera) 
madzulo Ndi m'mawa". 

42. Ndipo (kumbukira) pamene 
angelo adati: "E I we Mariam! 
Ndithudi, Mulungu Wakusankha, 
Wakuyeretsa ndipo 
Wakulemekeza, mwa Akazi onse 
amitundu ya anthu". 









®i 



Hy* 



V/f/ >i'*' 









1 Apa patchulidwa nkhani ya mayi Mariam (Maria) pomwe adatha msinkhu ndi 
pomwe mngelo adamuuza nkhani yabwinoyi. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



118 



r fjA-i 



T Olj-<kP JT 5jj-- 



43. "E iwe Mariam, 
dzichepetse Kwa Mbuye wako ndi 
Kumlambira powerama pamodzi 
Ndi owerama". 

44. Izi ndizina mwankhani 
zobisika zomwe 

Tikukuvumbulutsira. Sudali nawo 
pamene Amaponya zolembera 
zawo (m'madzi m'njira Ya 
mayere) kuti aone ndani mwaiwo 
alere Mariam. Sudali nawo 
pamene adali kutsutsana. 

45. (Kumbukira) pamene 
mngelo adati: "E iwe Mariam 
(Maria)! Mulungu akukuuza 
nkhani Yabwino (kuti ubereka 
mwana popanda Mwamuna Koma 
kupyolera mu) liwu lochokera 
Kwa lye (Mulungu, lakuti, 
"Bereka," ndipo Nkubereka 
Popanda kupezana ndi mwamuna). 
Dzina lake ndi Mesiya Yesu 
mwana wa Mariya, adzakhala 
wolemekezeka padziko lapansi ndi 
pa Tsiku lachimaliziro; ndiponso 
ndi mmodzi wa Oyandikitsidwa 
kwa Mulungu. 

46. "lye adzayankhula ndi anthu 
Ali mchikuta ndi kuukulu (Wake). 
Ndipo adzakhala Mmodzi wa 
anthu abwino". 

47. (Mariam) adati: "Mbuye 
wanga! Ndingakhale ndi mwana 
Bwanji pomwe sadandikhudze 
Munthu aliyense (mwamuna)?" 



(A^\>&2&\£& 



®£s*w\Z* 


















Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



119 



r *>» 



T Oij^P JT ojj-*» 



© u^c/^0 cl^^^^^l 



i^^\SC&\Ki& 



" l,? * 






(Mngelo) adati: "Ndi Momwemo. 
Mulungu Amalenga chimene 
wafuna. Akafuna chinthu 
amachiuza: "Chitika," ndipo 
chimachitikadi. 

48. Ndipo Mulungu 
adzamphunzitsa Kulemba, nzeru, 
Taurat ndi Injili. 

49. "Ndipo (adzamchita 
kukhala) Mneneri Kwa ana a 
Israeli (adzakhala akuwauza kuti): 
"Ine ndakudzerani ndizizindikiro 
kuchokera Kwa Mbuye wanu kuti 
ndikuumbireni dongo Ngati 
chithunzi chambalame, nkuuzira 
M'menemo nkukhaladi mbalame 
Mwachilolezo cha Mulungu; 
Ndipo ndichiritsa osapenya 
chibadwire, Ndiwamangamaanga, 
ndi kuukitsa wakufa Mwa 
chilolezo cha Mulungu; ndipo 
ndikuuzani Zomwe mudye ndi 
zimene musunge m'nyumba 
Zanu.Ndithudi, m'zimenezi muli 
zizindikiro Kwa inu ngati mulidi 
anthu okhulupirira. ! 

50. "Ndipo (ndikhala) 
wotsimikizira zomwe Zidalipo 
patsogolo panga (m'Buku la) 
Taurat. Ndipo ndadza kuti 
ndikulolezeni Zina mwa zomwe 
zidaletsedwa kwa inu. Ndipo 

1 Apa akunena zina mwazozizwitsa zomwe Mneneri Isa (Yesu) anadza nazo. 
Ndipo zina mwaizo ndikuumba ndidongo chifanizo chambalame. Kenako 
nkuchiuzira chikhaladi mbalame yamoyo mwachilolezo cha Mulungu. 



iKitf'Y' 9&>< 9. 9 9*{s >\Z\\~'9"S 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



120 r*>i. 



T OIj^p JT Sjj-- 



ndakudzerani ndi zizindikiro 
Kuchokera kwa Mbuye wanu 
(zotsimikizira Uthenga wanga). 
Choncho, opani Mulungu ndi 
kundimvera (ine). 

51. "Ndithu Mulungu ndiye 
Mbuye wanga ndiponso Mbuye 
Wanu; choncho mupembedzeni. 
Iyi ndiyo njira yoongoka". 

52. Koma pamene Yesu 
adazindikira mwa iwo 
Kusakhulupirira adati: "Ndani 
akhale athandizi Anga kwa 
Mulungu (popitiriza kufalitsa 
Chipembedzo Chake)?" Ophunzira 
ake Adati: "Ife ndife athandizi a 
Mulungu (pofalitsa Chipembedzo 
Chake). Takhulupirira Mulungu; 
ndipo ikira umboni kuti ife ndithu 
Ndi odzipereka (kwa Mulungu). 

53. "Mbuye wathu! 
Tazikhulupirira Zimene 
mwavumbulutsa, Ndipo tamtsata 
Mtumikiyo. Choncho tilembeni 
pamodzi Ndi oikira umboniwo." 

54. Ndipo (Ayuda) adakonza 
chiwembu (chofuna Kupha Yesu) 
Mulungu adachiwononga 
Chiwembu chawocho. Mulungu 
ngokhoza bwino zedi Poononga 
ziwembu za anthu a chiwembu. 

55. (Kumbukirani) pamene 
Mulungu adati: "Iwe Yesu! Ine 
ndikukwaniritsira nyengo yako 















aS32ill5**&l^ 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 121 ? ^j** 1 



T &\j»& JT ijj«* 



Yokhala ndi moyo. (Ayuda sachita 
kanthu Kwa iwe). Ndipo 
ndikunyamulira kwa Ine 
Ndikuyeretsa kwa anthu 
osakhulupirira (omwe Ndi adani 
ako). Ndipo amene akutsata (Iwe) 
Ndiwasankha kukhala apamwamba 
pa amene Sadakhulupirire kufikira 
tsiku lachimaliziro. Kenako 
kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo 
Ndidzaweruza pakati panu 
pazomwe mudali Kusiyana. 

56. Tsono amene 
sadakhulupirire, Ndiwakhaulitsa 
ndi chilango chaukali padziko 
lapansi ndi tsiku lomaliza, ndipo 
Sadzapeza athandizi. 

57. Koma amene akhulupirira 
Nachita zabwino, (Mulungu) 
adzawalipira malipiro Awo 
(mokwanira). Ndipo Mulungu 
Sakonda anthu ochita zoipa. 

58. Izi tikukuwerengera iwezi 
Ndi zivumbulutso ndi ulaliki 
waluntha. 

59. Ndithudi, fanizo la Yesu 
kwa Mulungu lili ngati fanizo la 
Adam; adamulenga ndi dothi 
namuuza kuti: "Khala munthu," 
Ndipo adakhaladi. 1 









9 k 9 u 



©4^ 



i4$&?£>&)&i 






1 (Ndime 59-62) Ndime iyi idavumbulutsidwa pamene nthumwi za chikhirisitu 
zidadza kwa mtumlki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuchokera ku 
Najirani. Iwowo adakangana ndi Mtumiki wa Mulungu pa nkhani ya Yesu. Iwo 
adati kwa Mtumiki wa Mulungu "Bwanji iwe ukutukwana Mneneri wathu?" lye 
adati: "Kodi ndikutukwana chotani?" Iwo adati: "Iwe ukuti iyeyo ndikapolo wa 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



122 



r *>i 



T ti\y>* JT Ojj-a 



60. (Ichi ndi) choona 
chochokera Kwa Mbuye wako; 
choncho Usakhale mwaokaikira. 

61. Ndipo amene akutsutsana 
nawe (Iwe Mtumiki) tsopano pa 
ichi Pambuyo pokudzera 
kuzindikira, Auze, "Bwerani 
tiitane ana athu ndi Ana anu, akazi 
athu ndi akazi anu, Ife ndi inu; 
kenako modzichepetsa Tipemphe 
temberero la Mulungu Kuti likhale 
pa amene ali Abodza (Mwa ife)." 

62. Ndithu, iyi ndinkhani 
yoona; ndipo palibe Woyenera 
kupembedzedwa mwa choonadi 
Koma Mulungu mmodzi. 
Ndithudi, lye Mulungu 
Ngwamphamvu Zoposa, 
Ngwanzeru zokuya. 

63. Ngati atembenuka 
(monyoza, Mulungu awakwapula); 









&CM$l&'&®)$$$ 



Mulungu." lye adati: "Inde. lyeyo ndi kapolo wa Mulungu ndiponso mawu ake 
omwe adawaponya mwanamwali." Zitatero iwo adapsa mtima ndipo 
anakwiya nati, "Kodi iwe udamuonapo munthu wobadwa popanda tate? Ngati 
ukunenadi zoona tationetsa munthu wotere." Apa mpomwe Mulungu 
adavumbulutsa ndime yakuti "Ndithudi, fanizo la Yesu (Isa) kwa Mulungu lili 
ngati fanizo la Adam". Kenako anawaitanira ku Chisilamu. Iwo adati: 
"Tidalowa kale m'Chisilamu iwe usanadze." Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye) adati: "Mwanama. Pali zinthu zitatu zikukuletsani kulowa 
m'Chisilamu: 

(a) Kunena kwanu mawu oti Mulungu wadzipangira mwana. 

(b) Kudya kwanu nyama ya nkhumba. 

(c) Kulambira kwanu mtanda." 

Pamene adapitiriza kumtsutsa Mneneri Muhammad (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye) adawapempha kuti atembererane ponena kuti, "O! Ambuye 
Mulungu! Mtemberereni ndi kumlanga amene akunena zabodza mwaife pankhani 
ya Yesu! Pompo Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adasonkhanitsa 
anthu ake. Koma iwo atakhala upo adagwirizana kuti asalole kuopa kuti 
chilango chingawatsikire. Potero zidadziwika kwa anthu kuti iwo ngabodza. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 123 T *>i 



T C)\j+fi> JT *jj*> 



Ndithudi Mulungu Ngodziwa za 
oononga. 

64. Nena: "Inu eni Buku (la 
Mulungu, Ayuda Ndi Akhrisitu!) 
Idzani kuliwu lolingana Pakati 
pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze 
Aliyense koma Mulungu Mmodzi 
Yekha), Ndiponso tisamphatikize 
ndi chilichonse; ena Mwa ife 
asawasandutse anzawo kukhala 
Milungu m'malo mwa Mulungu." 
Ngati atembenuka ndi kunyoza, 
nenani: "Ikirani umboni kuti ife 
ndife Asilamu (Ogonjera 
malamulo a Mulungu)." 

65. E inu amene mwapatsidwa 
Buku! Bwanji mukutsutsana za 
Ibrahim pomwe Taurat Ndi Injili 
sizidavumbulutsidwe Koma 
pambuyo Pake kodi 
simuzindikira? 

66. Taonani! Inu mudatsutsana 
pazomwe Mudazidziwa, nanga 
bwanji Mukutsutsana pazomwe 
simuzidziwa? Mulungu ndi 
Yemwe akudziwa. Pomwe inu 
simudziwa. 

67. Ibrahim sadali Myuda ndipo 
sadali Mkhrisitu, koma adali 
wolungama, Wodzipereka; ndipo 
sadali Mwa ophatikiza (Mulungu 
ndi zinthuzina) 

68. Ndithu anthu omwe ali 
oyenera Kudzilumikiza ndi 












Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



124 



r *>i 



T OI^*p JT Sjj^ 



M*'- 
!><* 






Ibrahim ndi amene Adamutsata 
(m'nyengo yake) ndi Mtumiki uyu 
(Muhammad {SAW}) ndi amene 
amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo 
Mulungu ndi Mtetezi wa 
okhulupirira. 

69. Gulu Una la anthu amene 
adapatsidwa Buku likufuna 
kukusokeretsani; Ndipo 
sasokeretsa aliyense koma Iwo 
wokha pomwe (iwo eni) 
Sakuzindikira. 

70. "E inu amene mwapatsidwa 
Buku! Bwanji mukuzikana 
Zizindikiro za Mulungu (Qur'ani) 
Pomwe mukudziwa? 

71. E inu amene mwapatsidwa 
Buku! Bwanji mukusakaniza 
Choona ndi chabodza, ndipo 
Mukubisa choona Uku 
mukudziwa? 

72. Ndipo gulu lina la amene 
adapatsidwa Buku lidati (kwa 
anzawo): "Khulupirirani chomwe 
Chavumbulutsidwa kwa Asilamu 
kumayambiriro Kwa usana, ndipo 
chikaneni Kumalekezero kwake 
(kwa usana) Mwina angabwerere 
(kusiya Chisilamu). 1 

1 Ena mwa anthu amabuku adalangizana pakati pawo kuti achikhulupirire 
chipembedzo cha Chisilamu nthawi zakummawa zokha. Ikakwana nthawi 
yopemphera Swala akapemphere nawo. Koma ikafika nthawi yamadzulo atuluke 
m'chipembedzocho ncholinga choti asokoneze Asilamu maganizo, makamaka 
omwe adali ofooka pomwe aone kuti anthu anzeru adalowa m'chipembedzocho, 
koma kenako atulukamo, nawonso mwina atuluka Poganiza kuti chikadakhala 



• iW'.'^S' 9 9 '?*1 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



125 r •>■» 



V OIjaP JT ijj^t 



73. Ndipo musakhulupirire 
aliyense Kupatula yekhayo yemwe 
watsata Chipembedzo chanu. 
(Mulungu Adauza Mtumiki 
{SAW}),nena:"Ndithudi, 
chiongoko chenicheni Ndi 
chiongoko cha Mulungu basi." 
(Amene adapatsidwa Buku 
Adanena kwa anzawo: 
"Musakhulupirire) kuti 
angapatsidwe Aliyense zofanana 
ndi zomwe Mwapatsidwa inu 
(Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti 
angakutsutseni Kwa Mbuye 
wanu." (Mulungu adati Kwa 
mtumiki { SAW} ), nena: "Ndithu, 
Zabwino zonse zili m'manja mwa 
Mulungu; amazipereka kwa 
Yemwe wamfuna. Mulungu 
Ndimataya, Ngodziwa." 

74. Amamsankhira chifundo 
Chake amene wamfuna. Ndipo 
Mulungu ndimwini Ubwino 
wawukulu. 

75. Mwa amene adapatsidwa 
Buku, Alipo omwe akuti 
ukawasungitsa Milumilu yachuma, 
akubwezera. Ndipo mwa iwo muli 
anthu ena akuti Ukawasungitsa 
"dinari" (ndalama) imodzi 
Sangakubwezere pokhapokha 
Upitirize kwa iye kuimirira 
kulonjerera. Izi Nchifukwa chakuti 









chipembedzo chenicheni anthu anzeru sakadatulukamo. Izi zidali ndale za 
Ayuda zomwe Mulungu adaziulula. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 



126 



r *j*-» 



y oij^p JT Sjj.*. 



amanena: "palibe njira Paife 
(yotidzudzulira) chifukwa 
chozibera Mbulizi." Koma 
akumnamizira Mulungu uku iwo 
akudziwa. 

76. Sichoncho (monga momwe 
akunenera)! Komaamene 
akukwaniritsa lonjezo Lake 
napewa Machimo (ndiyemwe 
Ayenera kukhala Wokondedwa 
Kwa Mulungu). Ndithudi, 
Mulungu amakonda opewa 
machimo. 

77. Ndithu anthu amene 
akugulitsa chipangano cha 
Mulungu ndi malumbiriro awo, 
(ndi zinthu za) Mtengo wochepa, 
iwo alibe gawo labwino pa Tsiku 
lomaliza. Ndipo Mulungu 
Sadzawayankhula (ndimawu 
abwino); Ndipo sadzawayang'ana 
(Ndi diso la chifundo) pa tsiku 
Lachimaliziro. Ndiponso 
sadzawayeretsa (Kumachimo 
awo); ndipo iwo Adzapeza 
chilango chopweteka. 

78. Ndipo ndithu mwaiwo muli 
gulu lomwe likukhotetsa malirime 
awo (powerenga) Buku kuti 
muaganizire (mawu awowo) Kuti 
ndi a m'buku La Mulungu); 
pomwe si am' buku (la Mulungu). 
Ndipo akunena: "Izi zachokera 
kwa Mulungu," Pomwe zimenezo 
sizinachokere kwa Mulungu; 



&4l&\$$ ufe<^&f <^<J 



e^l 









Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 127 T >>i 



T Otj^P JT 5jj-rf 



Ndipo akumnamizira Mulungu uku 
akudziwa. 

79. Sikoyenera kwa munthu 
yemwe Mulungu Wampatsa Buku 
ndi chiweruzo ndi uneneri, Kenako 
nanena kwa anthu: "Khalani 
opembedza Ine, mmalo mwa 
Mulungu." Koma (awauze): 
"Khalani opembedza Mulungu, 
anzeru, aluntha chifukwa choti 
mukuphunzitsa Buku ndi 
Chifukwanso chazomwe 
mukuphunzira. 

80. Ndipo sangakulamulireni 
Kuwasandutsa angelo ndi aneneri 
kukhala milungu. Kodi 
angakulamulireni Kusakhulupirira 
pambuyo Poti muli Asilamu? 

81. Ndipo (kumbukirani) 
pamene Mulungu adatenga 
Lonjezo kwa aneneri, 
(n'kuwauza): "Ndikakupatsani 
Buku ndi nzeru, nakudzerani 
Mtumiki wotsimikizira zomwe zili 
pamodzi Ndi inu, nkofunika kwa 
inu kumkhulupirira ndi 
Kumthangata." (Mulungu) 
adatinso: "Kodi mwavomereza ndi 
kulandira pazimenezi Pangano 
langali? (Iwo) adati: 
"Tavomereza". (lye) adati: "Tsono 
chitirani umboni, Ine ndili 
pamodzi nanu mwa oikira 
umboni." 



V • 9 $9 9S it 9 9s 






C^o «* 



fy feM53>i«Ui, O ^~*** Opt) 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 128 ? *j*-» 



T OIj^p JT 5jj^ 



82. Ndipo amene 
adzatembenuke Pambuyo pa 
lonjezoli, (Mulungu adzawalanga 
Chifukwa chakuti) iwo 
Ndiopandukiradi chilamulo Cha 
Mulungu. 

83. Kodi akufuna chipembedzo 
Chomwe si cha Mulungu pomwe 
Chinthu chilichonse chili 
Kumwamba ndipansi chikugonjera 
lye, mofuna kapena mosafuna? 
Ndipo onse adzabwezedwa kwa 
lye. 

84. Nena: "Takhulupirira 
Mulungu Ndi zomwe 
zavumbulutsidwa pa Ife, ndi 
zomwe zidavumbulutsidwa Kwa 
Ibrahim, ndi Isimail, Isihaka ndi 
Yakubu ndi zidzukulu Zake, ndi 
Zimene adapatsidwa Musa ndi 
Yesu, ndi aneneri (ena) Zochokera 
kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa 
aliyense pakati pawo, Ndipo ife 
kwa lye ndi Odzipereka 
kwathunthu." 

85. Ndipo amene angatsate 
Chipembedzo chosakhala 
Chisilamu, sichidzalandiridwa 
Kwa iye. Ndipo lye tsiku Lomaliza 
adzakhala mmodzi Mwa (Anthu) 
otaika. 

86. Kodi Mulungu 
angawaongole Bwanji anthu 
omwe atuluka M'chikhulupiriro 



^^M'i^'*'' 1 



>*^j?. 



9 1 9 






X 99 ' 9 9 









U^j^&^4&ltfl^<il!^ 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 3 129 f *>» 



T OIj^p JT djj-» 



pambuyo Pakukhulupirira 
natsimikiza Kuti Mtumiki (Uyu 
Muhammad {SAW}) Ngoona, 
nkuwafikiranso zisonyezo 
Zoonekera? Koma Mulungu 
saongola Anthu ochita zoipa. 

87. Iwo mphoto yawo Ndithu 
ndi matemberero A Mulungu, a 
angelo ndi Anthu onse, ali Pa iwo. 

88. M'menemo adzakhala 
muyaya; Ndipo 

sichidzapeputsidwa Chilango kwa 
iwo, Ndiponso sadzapatsidwa 
danga. 

89. Kupatula anthu amene 
alapa, Pambuyo pazimenezo 
Nachita zabwino. Ndithudi, 
Mulungu Ngokhululuka, 
Ngwachisoni. 

90. Ndithudi, anthu amene 
Atuluka M'chikhulupiriro 
pambuyo Pokhulupirira, kenako 
Naonjezera kusakhulupirira, 
Kulapa kwawo 
sikudzavomerezedwa Konse. 
Ndipo iwo ndi osokera. 

91. Ndithudi amene 
sadakhulupirire, Nkumwalira 
pamene ali Osakhulupirira, 
sikudzalandiridwa Kwa aliyense 
wa iwo ngakhale Atapereka dipo 
lagolide lodzadza Padziko lonse. 
Iwo ndi Omwe adzalandire 









®, 



'ta 









©£$12)^ 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



130 



£ >>» 



V OIj^p JT Sjj-> 



chilango Chopweteka, ndipo 
sadzakhala Ndi athandizi. 

92. Simudzapeza ubwino 
(weniweni) kufikira mutapereka 
zimene mukuzikonda. Ndipo 
chilichonse chimene mupereka, 
Ndithudi, Mulungu akuchidziwa. 

93. Zakudya zonse zidali 
zololedwa Kwa ana a Israeli 
kupatula Chimene adadziretsa 
Israeli mwini wake Taurat 
Isadavumbulutsidwe. Nena: 
"Bwerani ndi Tauratiyo ndipo 
Iwerengeni ngati mukunena 
zoona." 1 

94. Ndipo aliyense amene 
Adzapekera bodza Mulungu 
pambuyo Pa izi iwo Ndiwochita 
zoipa. 

95. Nena: "Mulungu wanena 
zoona. choncho tsatirani 
chipembedzo cha Ibrahim yemwe 
adali Wolungama; sadali mwa 
ophatikiza (Mulungu ndi 
mafano)." 

96. Ndithudi, Nyumba yoyamba 
Yomwe idakhazikitsidwa chifukwa 






uJfr 









'&£$omi4&$& 



Ayuda adauza Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti, "Iwe 
sukutsata chikhalidwe cha Ibrahim ngakhale umadzinyenga kuti ukumtsata. 
Nanga bwanji ukudya nyama yangamira, pomwe Mneneri Ibrahim sadali kudya 
ngamira?" Apa Mulungu akuwatsutsa kuti ngabodza. Ndipo Buku lawo la Taurat 
ndilo mboni pabodza lawoli. Atavundukula Buku lawo la Taurat apeza kuti yemwe 
adadziletsa kudya ngamira ndi Yakobo, yemwe ankadziwikanso kuti Israeli, osati 
Mneneri Ibrahim. Yakobo njemwe adasala kudya nyama yangamira mwachifuniro 
chake. Ndipo izi adazichita popanda kukakamizidwa ndi Mulungu. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 131 * *>' 



T OIj^p JT 5jj^ 



cha anthu (kuti azipempheramo) 
ndiyomwe Hi m'Makka; 
yodalitsidwa Ndiponso ndi 
chiongolo Kwa anthu onse. 1 

97. M'menemo muli zizindikiro 
zoonekera (Zozindikiritsa 
kupatulika kwake ndi Ukale 
wake); ndi pamalo pom we Ibrahim 
Adali kuimirira; ndipo amene 
akulowamo Amakhala 
m'chitetezo; ndipo Mulungu 
Walamula anthu kuti akachite Hija 
ku Nyumbayo amene angathe 
kukonzekera Ulendo wonka 
kumeneko. Ndipo Yemwe 
angakane, (osapitako Pomwe ali 
nazo zomuyenereza), Ndithudi, 
Mulungu Ngwachikwanekwane Pa 
zolengedwa Zake. 

98. Nena: "E inu amene 
mudapatsidwa Buku! chifukwa 
chiyani Mukuzikana zizindikiro Za 
Mulungu pomwe Mulungu ndi 
mboni wazonse Zimene 
mukuchita?" 

99. Nena: " E inu amene 
mudapatsidwa Buku! chifukwa 
chani mukutsekereza Anthu amene 
akhulupirira kuyenda Panjira ya 
Mulungu? Mukufuna kuti Ikhote 
pomwe inu ndinu mboni (Kuti ndi 



s> iMr **K *&'}* 



*w&m> 












1 Apa akunenetsa kuti nyumba yoyamba kukhazikitsidwa kwa anthu kuti ikhale 
yochitira mapemphero ndi Al-Kaaba, osati Baiti Mukadasi monga momwe Ayuda 
amakhulupirira. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



132 i ►>• 



T OIjaP JT ojj»- 



• *' 9 fa 9 *)' "" J.f&tt'W " • uTl ' W 









njira ya Mulungu Yopanda 
choipa)? Komatu Mulungu 
Sanyalanyaza zomwe mukuchita." 

100. E inu amene 
mwakhulupirira! Ngati 
muwamvera ena Mwa amene 
apatsidwa Buku, akubwezani kuti 
Mukhale osakhulupirira Pambuyo 
pa chikhulupiriro chanu. 

101. Kodi mungakhale 
osakhulupirira Bwanji pomwe 
ndime za Mulungu 
zikuwerengedwa kwa Inu, 
pomwenso Mtumiki wake ali 
pamodzi nanu? Ndipo amene 
Agwiritse mwa Mulungu 
(Bwinobwino), ndithudi iye 
Wawongoleredwa kunjira 
yoongoka. 

102. E inu amene 
mwakhulupirira! Opani Mulungu; 
Kuopa Kwenikweni. Ndipo musafe 
Pokhapokha mutakhala Asilamu 
(ogonjera). 1 

103. Ndipo gwiritsani chingwe 
(Chipembedzo) Cha Mulungu 
nonsenu, ndipo Musagawikane. 
Kumbukirani Mtendere wa 
Mulungu womwe Uli painu; 
pamene mudali odana Ndipo Iye 

1 Pandime iyi akulangiza kuti nthawi iliyonse munthu akhale m'chikhalidwe cha 
Chisilamu chokwanira popewa zoletsedwa ndi kumachita zimene alamultdwa 
kuchita mmene angathere, chifukwa chakuti munthu sangadziwe nthawi imene 
imfa ingamufikire. 






*9 <. 9 \' 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 133 * *>* 



V d\y>* JT $jy* 



^i#jR&\{&&&®& 



S 9 9*is 



adalunzanitsa pakati Pamitima 
yanu, tero mwamtendere Wake 
mudakhala abale; ndipo Mudali 
m'mphepete mwa dzenje Lamoto 
(wa Jahanama), ndipo lye 
Adakupulumutsanimo. Umo ndi 
Momwe Mulungu 
akukufotokozerani Ma aya Ake 
(ndime Zake) kuti muongoke. 1 

104. Ndipo mwa inu lipezeke 
Gulu la anthu oitanira Kuzabwino 
(Chisilamu) Ndipo alamule 
(Kuchita) Zabwino ndikuletsa 
zoipa. Iwo ndiwo opambana. 

105. Ndipo musakhale monga 
Aja amene adagawikana Nasiyana 
pambuyo Powadzera zisonyezo 
Zoonekera poyera (Zowaletsa 
kutero). Ndipo Iwo adzakhala 
Ndichilango chachikulu. 

106. Patsikulo nkhope zina 
zidzakhala Zowala pomwe nkhope 
zina zidzakhala Zakuda. Tsono 
amene nkhope zawo Zidzakhala 
zakuda, (adzauzidwa): "Kodi 
Mudakana ( Mulungu) pambuyo 
Pachikhulupiriro chanu? Choncho, 
Lawani chilango (Chopweteka) 
Chifukwa cha zomwe mudali 
kuzikana." 



1 Ndime izi zikuwauza Asilamu onse kuti akhale ogwirizana pamodzi m'dzina 
lachipembedzo chawo cha Chisilamu. Asapatukane popatsana maina atsopano 
kapena kuti awa akuchokera kudziko lakutilakuti, awa ngamtundu wakutiwakuti. 
Kuchita zimenezo nkulakwa kwambiri. Koma pakati pa Asilamu pakhale 
chimvano. 









Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



134 



t *>i 



T ti\j+* JT 5jj-- 



107. Tsono (anthu odala) omwe 
nkhope zawo zidzawale, adzakhala 
m'chifundo cha Mulungu. Iwo 
mmenemo adzakhala muyaya. 

108. Awa ndi ma aya (ndime) A 
Mulungu; tikukuwerengera 
Mwachoonadi. Ndipo Mulungu 
Safuna kupondereza Zolengedwa 
(zake). 

109. Chilichonse cha 
kumwamba Ndipansi ncha 
Mulungu. Ndipo Zinthu zonse 
zidzabwezedwa Kwa Mulungu. 

110. Inu (Asilamu) ndinu 
mpingo wabwino umene 
wasankhidwa kuti uchite zokomera 
anthu (onse). Mukulamula 
(kuchita) zabwino ndi kuletsa 
zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa 
Mulungu. Ndipo aja adapatsidwa 
Buku Akadakhulupirira monga 
momwe (Adawalamulira) 
kukadakhala kwabwino Kwa iwo. 
(Koma) mwa iwo alipo 
okhulupirira pomwe ambiri 
mwaiwo Ngopandukira 
(chilamulo cha Mulungu). 1 

111. Sangakuvutitseni (adani 
anuwo, Makamaka Ayuda) koma 
nditimasautso (tochepa); ngati 
(Atayesera) kukuthirani nkhondo, 
Akufulatirani (kuthawa); ndipo 
Kenako sangapulumutsidwe. 



-'Xt 9*\ l» h ??9 9 4'Il S'.Zir'ls 












Apa akutchula zifukwa zomwe chipembedzo cha Chisilamu chapambanira 
zipembedzo zina. Tero tiyeni tigwirizane ndizimenezi kuti tikhaledi opambana. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 135 * *>' 



T d\y>* JT 5jj-rf 












% 'A 



%^\c£\&&\*& 



e^l&I^U 



112. Adindidwa chidindo 
chakunyozeka paliponse pamene 
angapezeke kupatula (akagwira) 
Chingwe (cha chipembedzo) cha 
Mulungu, Kapena chingwe cha 
anthu (pothandizidwa Ndi anthu 
ena. Koma paokha sangakhale ndi 
Nyonga). Abwerera ndi mkwiyo 
wa Mulungu; ndipo chidindo 
chaumphawi Chadindidwa paiwo. 
Izi nchifukwa chakuti Iwo sadali 
kukhulupirira mawu a Mulungu, 
Ndipo amapha aneneri popanda 
choonadi. Izi nchifukwa chakutinso 
adanyoza Ndikulumpha malire. 

113. Iwo amene adapatsidwa 
Buku sali ofanana. Mwa iwo muli 
anthu olungama omwe 
akuwerenga ma aya (ndime) a 
Mulungu nthawi za usiku uku 
akumulambira. 

114. Amakhulupirira Mulungu 
ndi Tsiku lomaliza; ndipo 
amalamulira (kuchita) zabwino 
ndikuletsa zoipa; ndipo amachita 
changu pazinthu zabwino. Ndipo 
iwo ndi omwe Ali mwa anthu 
abwino. 

115. Ndipo chabwino 
chilichonse chimene angachite 
sadzakanidwa nacho, (koma 
adzawalipira malipiro abwino). 
Ndipo Mulungu ngodziwa za 
amene akuopa lye. 1 

1 Apa akunenetsa kuti aliyense amene akuchita zabwino ndicholinga chabwino 
ndi kutsata lamulo la Mulungu, adzalipidwa pa zabwino zakezo. 






* S9*9" .99>'\\ ' *99 9 rs 



®i 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



136 



i *j*-l 



T OIj*p JT ijy* 









116.Ndithudi, amene 
sakhulupirira, chuma chawo 
ngakhale ana awo, 
sizidzawathandiza chilichonse kwa 
Mulungu. Ndipo Iwo ndi anthu 
akumoto basi; adzakhala 
mmenemo muyaya. 

117. Fanizo la chimene 
akupereka mwaulere pamoyo uwu 
wadziko lapansi, chili ngati 
mphepo yomwe mkati mwake muli 
chisanu chaukali, chagwera 
pamunda wa anthu omwe 
adadzichitira okha zoipa, 
N'kuonongeratu. Si Mulungu 
amene adawachitira zoipa, koma 
iwo okha adadzichitira zoipa. 1 

118. E inu amene 
mwakhulupirira! musawachite 
omwe sali mwa inu kukhala 
abwenzi; owauza chinsinsi, iwo 
sasiya kukuchitirani choipa. 
Amakonda zimene 
zikukuvutitsani. Chidani chawo 
(painu) chaonekera M'milomo 
yawo. Ndipo zimene zikubisa 
zifuwa zawo, nzazikulu zedi. 
Ndithudi, takufotokozerani 
zizindikiro zonse ngati inu muli 
anthu ozindikira. 2 



1 Tsono amene savomereza Mulungu potsatira malamulo ake ndikusiya zomwe 
lye adaletsa, ngakhale atachita zabwino zotani sakamlipira pa tsiku lomaliza. 
Ngati nkofunika kuti amlipire, ndiye kuti amlipiriratu pompano padziko lapansi. 

2 Chimodzi mwa zinthu zazikulu chomwe chimachititsa kuti zochita za anthu 
zitheke kapena kuti zilongosoke, ndiko kuzikonza zinthuzo mwachinsinsi. Zioneke 






Sural 3. Al-'Imran Juzu 4 



137 



i *jA-i 



T JIjaP JT 5jj-- 



119. Ha! kodi inu ndinu amene 
muwakonda (adani anu) pomwe 
iwo sakukondani ngakhale inu 
mukukhulupirira mabuku onse? 
Akakumana nanu amanena 
(mwachiphamaso) : 
"Takhulupirira." Koma akakhala 
kwaokha, amakulumirani nsonga 
za zala chifukwa chaukali. Nena: 
"Mwalirani ndiukali wanuwo 
ndithudi, Mulungu akudziwa za 
m'zifuwa (mwanu)." 

120. Ngati chabwino 
chikakufikirani, amaipidwa nacho; 
koma choipa chikakugwerani 
amachikondwerera koma ngati inu 
mupirira ndi kuopa Mulungu, 
ndale zawo sizingakuvutitseni 
chilichonse. Ndithu Mulungu 
akudziwa bwino zonse zimene iwo 
akuchita. 1 

121. (Kumbukira) pamene 
unachoka M'mawa kusiya banja 
lako kuti uwakonzere Asilamu 
malo omenyanira (nkhondo). ndipo 









h*'L 'n 9 '\ 






pamaso pa anthu zili zothaitha kuzikonza. Chifukwa pali anthu ambiri oipa 
maganizo omwe safuna kuti zinthu za anzawo zilongosoke. Iwo amafunitsitsa kuti 
aziononge zisanachitike. Ndipo nchifukwa chake apa akuletsa kuwaululira 
zachinsinsi anthu omwe sali Asilamu, kapena kuwachita kukhala abwenzi enieni. 
Komatu sikuti apa akuletsa ubwenzi wakuti, "Muli bwanji? Tin bwino". Ndiponso 
sakuletsa kuwachitira zabwino ndi zachilungamo, monga momwe afotokozera 
pandime yachisanu nchitatu yam'surat Mumtahina. (Qur'an 60:8) 

M'ndime iyi akuwauza kuti asaope ufiti ngakhale kulodzedwa. Koma ayadzamire 
kwa Mulungu basi. Chimene Mulungu wafuna chimachitika. Palibe amene 
angachitsekereze. Choncho m'bale wanga moyo wako ukhale wokhazikika. Ngati 
ufuna kuchita chinthu usaope mfiti, wadumbo ndi mdani. Dziwa kuti chimene 
Mulungu walemba sichingafafanizidwe. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 138 * *>» 



T Jlj^P JT Ojj-* 



Mulungu Ngwakumva, Ngodziwa. 

122. (Kumbukira) pamene 
magulu awiri mwa inu 
anafiinitsitsa kuti athawe 
(chifukwa cha mantha monga 
momwe adathawira achinyengo). 
Koma Mulungu adali Mtetezi 
wamagulu awiriwo. (Choncho 
adawasunga kuti asathawe). Ndipo 
asilamu ayadzamire kwa Mulungu 
yekha basi. 

123. Mulungu 
adakupulumutsani pa (nkhondo) ya 
Badri pomwe inu munali ofooka 
(chifukwa chakuchepa ndi 
kusakhala ndi zida zokwanira). 
Choncho opani Mulungu kuti 
mumthokoze (nthawi zonse 
pazomwe akukuchitirani). 

124. (Kumbukira) pamene 
umauza Asilamu: "Kodi 
sizikukukwanirani pokuonjezerani 
mbuye wanu zikwi zitatu Za 
Angelo otsitsidwa? 2 












1 Apa akunena nkhani ya nkhondo yachiwiri yaikulu kwabasi pambiri ya 
Chisilamu, nkhondo ya Uhudi. Nkhondo imeneyi Asilamu adalephera kwakukulu 
chifukwa cha Asilamu ena amene adaswa lamulo la Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye). Ndiponso chifukwa cha anthu ena omwe adalowa 
Chisilamu mwachiphamaso (Amunafikina), omwe adapita kunkhondo pamodzi ndi 
Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) koma adakathawa kunkhondoko. 
Ndipo adali ochuluka chigawo chimodzi mwa zigawo zitatu za Asilamu ( V3). 
Pothawapo adathawa ochuluka kuposa nambala yatchulidwayi. Koma ena mwa 
iwo adabwerera nkudzalumikizananso ndi gulu la nkhondo la Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye). 

2 M'ndime iyi akunena kuti Asilamu pankhondo zawo zolimbana ndi anthu 
osakhulupirira Mulungu, adali kuthandizidwa ndi magulumagulu a Angelo. 
Angelowo amadza monga anthu ndipo amamenya nkhondo ndi mphamvu 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



139 



t *>i 



T OIj^p JT 5jj^» 



125. "Inde, ngati mupirira ndi 
kudziteteza kumachimo, ndipo 
(adani anu) nakudzerani 
mwachangu chawo chimenechi 
pamenepo Mbuye wanu 
adzakuonjezerani ndi zikwi zisanu 
za Angelo odziwa kumenya 
nkhondo." 

126. Ndipo Mulungu sadachite 
izi (potumiza angelo) koma kuti 
ukhale uthenga wabwino kwainu 
ndi kuti pakutero mitima yanu 
ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo 
chithandizo sichichokera (kwa 
wina aliyense) koma kwa Mulungu 
basi, Wamphamvu zoposa, 
Wanzeru zakuya. 

127. (Kuchita izi) nkuti adule 
gawo la osakhulupirira (kuti ena a 
iwo aphedwe) kapena awasambule 
ndi kuti abwerere ali olephera. 1 

128. Iwe ulibe chako pa izi. 
Mwina (Mulungu) angalandire 
kulapa kwawo kapena kuwalanga 
pakuti iwo ndi anthu oipa. 

129. Zonse zakumwamba ndi 
zapansi nza Mulungu; 












zaumunthu, osati zaungelo. Akadamenya nkhondoyo ndimphamvu yaungelo 
ndiye kuti mngelo mmodzi yekha akadawamaliza osakhulupirira onse psiti. 
1 (Ndime 127-8) Apa Mulungu akufotokoza zifukwa zomwe adapambanitsira 
Asilamu. Ndipo akusonyeza ufumu wake kuti chimene lye wachifuna nchomwe 
chingachitike, osati chomwe auje ndi auje akufuna, ngakhale Mtumiki amene. 
Ngabodza omwe amati chimene akutiakuti afuna chimachitika, eti chifukwa choti 
iwowo ngolungama kwa Mulungu, kapena chifukwa chakuti ngoyera. Izi sizoona. 



Surat 3. Al- 4 Imran Juzu 4 



140 



i *j*-i 



V CMjaP JT ijj~* 



amamkhululukira amene wamfuna, 
ndikumulanga amene wamfuna. 
Komatu Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachisoni. 

130, E inu amene 
mwakhulupirira! Musadye Riba 
(chuma cha katapira), 
Kumangoonjezeraonjezera. Ndipo 
opani Mulungu Kuti mupambane. 1 

131, Ndipo opani moto umene 
Wakonzedwa kwa (Anthu) 
osakhulupirira. 

132, Ndipo mverani Mulungu 
Ndi Mtumiki Kuti mumveredwe 
chisoni. 

133, Ndipo chimkereni 
mwachangu chikhululuko Cha 
Mbuye wanu (kupyolera m' zochita 
zanu Zabwino), ndi Munda (wake) 
umene Kutambasuka kwake 
(mulifupi) Kuli ngati kumwamba 
ndi pansi, Worn we wakonzedwa 
kuti Ukhale wa oopa Mulungu. 3 



1 Kuipa kwina kwa malonda akatapira (Riba) ndiko kuti amangoonjezeraonjezera 
mpaka kuchimaliza chuma chamnzakeyo momchenjerera. Ndipo nchifukwa 
chake m'ndime yachiwiriyi ya 131 akunenetsa kuti ngati sasiya machitidwe 
akatapira (Riba) ndi kubweza kwa eni zomwe adalandazo, moto wa Jahanama 
ukuwadikira. 

2 M'ndime iyi akufotokozamo kuti chifundo cha Mulungu sichingapezeke 
pokhapokha pomumvera Mulungu ndi Mtumiki wake, potsatira malamulo ake ndi 
kupewa zoletsedwa. Munthu sakalowa mumtendere chifukwa choti ndi Msilamu 
basi. Kapena chifukwa chakuti amatsata njira yakutiyakuti . Kapena kuti 
mtsogoleri yemwe adayambitsa njirayo akakuombola pomwe zochita zake zili 
kutali ndimalangizo a Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye). Palibe 
angathe kukuombola koma zochita zako zabwino ndizo zidzakuombole. 

3 Ndime iyi ikulimbikitsa anthu kuti akangaze kuchita zinthu zowapezetsa chikondi 
cha Mulungu. 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 141 * *>* 



T My** JT 6jy* 



134. Omwe amapereka 
(zopereka Zawo mwaulere) 
pamene akupeza bwino Ngakhale 
pamene akuvutika; amenenso 
Amabisa ukali wawo ndi 
okhululukira Anthu. Ndipo 
Mulungu Amakonda ochita 
zabwino. 1 

135. Ndi amene amati akachita 
Uve (wamachimo), Kapena 
kudzichitira okha zoipa, 
Amakumbukira Mulungu 
nampempha Chikhululuko pa 
machimo awo. Palibe 
angakhululuke machimo Koma 
Mulungu ndipo Napanda 
kupitiriza machimo Omwe achita 
uku akudziwa . 

136. Iwowo mphoto yawo ndi 
Chikhululuko chochokera kwa 
Mbuye wawo, Ndi minda yoyenda 
mitsinje pansi pake Ndi patsogolo 
pake, momwe akakhalamo Mpaka 
muyaya. Taonani kukoma malipiro 
A ochita zabwino. 

137. Zidapita njira za zilango 
zambiri Zosiyanasiyana zomwe 
adapatsidwa amene Adalipo 
patsogolo panu. Tero tayendani 
Padziko ndi kuona momwe adalili 
mapeto a Anthu otsutsa. 

138. Uku ndi kulengeza poyera 
kwa anthu (Onse); komanso 












{ 9?9 <ty< 9 9> i*4 9 * '? 'C 



®c. 



\l^Atfiiu£S<3St&i 



1 (Ndime 134-5) Ndime izi zikutchula ena mwamakhalidwe omwe munthu 
atakhala nawo akalowa kumunda Wamtendere. 



Siirat 3. Al-'Imran Juzu 4 



142 



i tj^\ 



T d\j+* JT 3jj-*» 



chiongoko ndi ulaliki Kwa (anthu) 
oopa Mulungu! 

139.Ndipo musafooke 
(pomenya nkhondo), ndiponso 
Musadandaule (ndi mavuto amene 
akupezani) Pakuti ndinu 
apamwamba, Ngati mulidi 
okhulupirira. 

140. Ngati mwavulazidwa, 
naonso anthuwo Avulazidwanso 
molingana. Ndipo masiku 
(Amavuto) onga awa timawapatsa 
anthu Mosinthanasinthana. (Ichi 
chachitika) kuti Mulungu aonetse 
poyera amene akhulupirira 
(Moona; choncho sadathawe 
konse); ndi kuti Awachite ena 
mwa inu kukhala Shuhadaa (Ofera 
pankhondo yoyera). Komatu 
Mulungu Sakonda anthu ochita 
zoipa. 1 

141. (Izi) nkuti Mulungu 
awayeretse Amene akhulupirira 
Ndikuwathetseratu osakhulupirira. 

142. Kodi mukuganiza kuti 
mukalowa Kumunda wamtendere 
pomwe Mulungu asadawaonetsere 
Poyera amene amenyera 
chipembedzo Cha Mulungu 
mwainu ndi Kuwaonetseranso 















1 M'ndime iyi Mulungu akukumbutsa Asilamu zinthu zosowetsa mtendere zomwe 
zidawapeza m'masiku a Uhudi powauza kuti monga iwo adavutitsidwa ndi adani 
awo, nawonso adavutitsidwa . Umo ndi momwe zinthu zimachitikira 
mosinthasintha. Nthawi zina zigwera awa, kenako zigwera ena, malinga ndi 
zochita zawo. Mulungu sakondera. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 143 * *>* 



V &\j+* JT ijj*t 



poyera Opirira (pankhondo ya 
Mulungu?) 1 

143.Ndithudi, mudali 
kuilakalaka Imfa musanakumane 
nayo. Ndithudi tsopano mwaiona 
(Ndikuphedwa kwa abale anu) Inu 
mukupenya. 2 

144. Muhammad (SAW) sali 
chinthu China koma Mtumiki 
chabe. Patsogolo pake adamuka 
atumiki Ambiri. Kodi ngati 
atamwalira kapena Kuphedwa, 
mungabwererenso M'mbuyo, 
ndipo amene abwerere M'mbuyo 
mwake savutitsa Mulungu ndi 
chilichonse; Koma Mulungu 
Adzalipira othokoza. 

145. Munthu aliyense sangafe 
Pokhapokha mwa chilolezo Cha 
Mulungu, (ndikukwanira) Nthawi 
yake yolembedwa. Ndipo amene 
akufuna mphoto Yapadziko 












"*s 






1 Ndime iyi yikusonyeza chifukwa chomwe Mulungu adalekerera Asilamu kuti 
agonjetsedwe pankhondo ya Uhudi. 

2 Pamene Asilamu adamva ubwino waukulu umene angaupeze akafera 
pankhondoyo monga "Shahidi", aliyense waiwo adakhumba akadafera 
pankhondo yoteroyo, kuti akapeze ulemererowo. 

Choncho Asilamu makumi asanu ndi awiri (70) adaphedwa pankhondo ya Uhudi 
mwa anthu mazana asanu ndi awiri (700) omwe adaima mwamphamvu 
kulimbana ndi anthu osakhulupirira omwe adalipo zikwi zitatu (3,000). 

3 Apa akunena mwatsatanetsatane kuti Mneneri Muhammad (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) ndi mtumiki basi yemwe ndimunthu monga alili anthu ena 
onse. Adafa monga momwe ena adafera. Koma ngakhale iye wafa anthu ena 
atsanzire chikhalidwe chake ndi zophunzitsa zake zomwe amaphunzitsa. 
Asabwerere m'mbuyo poona kuti iye wafa. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



144 



t *>! 



T OIj^p JT 5jj-*» 



lapansi, timpatsa Pompo; ndipo 
amene akufuna Mphoto ya tsiku 
lomaliza tidzampatsa Konko. 
Ndithudi, tidzawalipira (Zabwino) 
othokoza. ] 

146. Ndi Aneneri angati 
adamenyana (Ndi adani) pamodzi 
ndi anthu Olungama ambiri 
komatu sadataye Mtima pamavuto 
omwe Adawagwera panjira ya 
Mulungu; sadafooke Ndipo 
sadagonjere (adani awo) Ndipo 
Mulungu amakonda opirira. 

147. (Anthu olungamawa) 
kunena kwawo sikudali Kwina 
koma ankati: "Mbuye wathu! 
Tikhululukireni machimo athu ndi 
kupyola Malire kwathu m'zinthu 
zathu. Ndipo Limbikitsani mapazi 
athu (panjira Yanu) Ndipo 
tithandizeni ku anthu 
osakhulupirira." 

148. Choncho Mulungu 
adawapatsa mphoto Yapadziko 
lapansi ndi mphoto yabwino Ya 
tsiku lomaliza. Mulungu amakonda 
Ochita zabwino. 

149. E inu amene 
mwakhulupirira! Ngati 
Muwamvere amene 



»a 



u^^V*^£^' 



© 






til \JJi\,J Gsy> i £3 l£*-\ 






\J^ &l\j^\ &£ 



m<&&&>$&$\ 



1 Apa akutilimbikitsa kuti tigwire ntchito yodzatipindulira pa tsiku lachiweruziro 
molimbika, tsiku lomwe ndilamoyo wosatha. 

2 Asilamu akuwauza kuti asataye mtima atawagonjetsa pankhondo iliyonse, 
kapena atawapeza masautso amtundu uliwonse. Chofunika nkupirira ndi 
kulimbana nawo mavutowo. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



145 



i *>» 



T d\j»e JT i^y* 



sadakhulupirire, Akubwezerani 
kumbuyo kwanu (Kumachitidwe 
achikunja) tero Mudzakhala otaika. 

150. Komatu Mulungu ndiye 
Mbuye wanu. lye Ngwabwino 
kwabasi kuposa Athandizi (ena 
onse). 

151. Tiponya mantha m'mitima 
mwa amene Sadakhulupirire 
chifukwa chakumphatikiza 
Mulungu (ndi mafano) omwe 
Mulungu Sadatsitsire umboni 
(wosonyeza umulungu Wawo) 
ndipo malo awo adzakhala 
kumoto. Taonani kuipitsitsa malo a 
anthu ochita zoipa. 

152.Ndithudi, Mulungu 
adakutsimikizirani Lonjezo lake 
(lakuti muwagonjetsa Adani). 
Choncho mudali kuwapha 
mwachilolezo Chake kufikira 
pamene mudafooka ndikuyamba 
Kukangana za lamulolo, tero 
mudalinyozera Pambuyo 
pokuonetsani zimene 
mumazikonda; (Pamenepo 
mpomwe adasiya kukuthangatani). 
Alipo ena mwainu amene 
akukonda dziko Lapansi 
(zamdziko), ndipo alipo ena 
mwainu Amene akukonda tsiku 
lomaliza. Kenako (Mulungu) 
adakuchotsani paiwo 
(adakusiitsani Kuwamenya 












Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



146 



t *>i 



V OI^aP JT 5jj-» 



osakhulupirirawo) kuti akuyeseni 
Mayeso. Koma lye tsopano 
wakukhululukirani. Ndipo 
Mulungu ndi mwini kuchita 
Zabwino paokhulupirira. 1 

153. Kumbukirani pamene 
mudali kuthawa Mwaliwiro 
popanda kumvera aliyense; 
Pomwe Mtumiki adali kukuitanani, 
ali Pambuyo panu. Ndipo 
(Mulungu) Adakupatsani 
madandaulo pamadandaulo. 
(Motero wakukhululukirani) Kuti 
musadandaule Pazomwe 
zakudutsani, ngakhalenso 
(Pamasautso) omwe akupezani. 
Ndipo Mulungu Ngodziwa Zonse 
zimene muchita. 

154. Kenako pambuyo 
pakudandaula, adakutsitsirani 
Mpumulo - tulo tomwe tidaphimba 
gulu Lina mwa inu. Padali gulu 



"I'll ' 'i\ ' S\" ** *i i i 






Apa akulongosola chifukwa chomwe Asilamu adagonjera. Iwo adagonja 
chifukwa choswa lamulo la Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) lomwe 
adawalamula. Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adaika paphiri anthu 
makumi asanu (50) omwe adali akatswiri olasa mipaliro. Adawauza kuti 
asachokepo kuti ateteze gulu la Asilamu kuti adani asawamenye nkhondo 
powadzerera kumbuyo. Adanenetsa kwa iwo kuti asachoke pamalopo ngakhale 
ataona kuti anzawo akupambana kapena akugonja, kufikira Mtumiki atawalamula 
kuti achokepo. Koma ena mwa iwo adanyoza lamuloli pamene adaona kuti 
anzawo chammunsi mwaphirilo akupambana ndipo akuthamangitsa adani ndi 
kuwapha ndikumatola zotolatola zapankhondo. Choncho, iwo anatsika paphiripo 
nkusakanikirana ndi anzawo nayamba kutola nawo zotola zapankhondo. 
Mtsogoleri wawo adayesera umu ndi umu kuwaletsa koma sadamumvere 
kupatula ochepa okha amene adatsala paphiripo. Pompo ngwazi zina zam'gulu la 
adani awowo zitaona kuti anthu omwe adali paphiri achokapo, zidalitembenuza 
gulu lawo lankhondo nkuyamba kuwamenya Asilamu chakumbuyo. Potero ambiri 
adaphedwa ndi kuvulala. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



147 



£*>i 



T Olj^P JT $jy* 






Una lomwe maganizo Awo 
adawatangwanitsa (kotero kuti 
Amangoziganizira okha) 
namuganizira Mulungu Ndi 
zoganizira zopanda choonadi, 
zoganizira Zaumbuli; ankati: "Ha! 
kodi tili ndi chiyani Ife pachinthu 
ichi?" Nena: "Zinthu zonse Nza 
Mulungu". Akubisa m'mitima 
mwawo Zomwe sakuzionetsa kwa 
iwe. Akunena: "Tidakakhala ndi 
chilichonse pachinthu ichi, Bwenzi 
sitikadaphedwa apa". Nena: 
"Ngakhale mukadakhala 
m'nyumba Zanu, ndithudi kwa iwo 
amene imfa idalembedwa (kuti 
amwalire) Akadapita kumalo 
omwalilirawo, Koma Mulungu 
(adachita izi) kuti Awonetse 
poyera zomwe zili M'zifuwa zanu. 
Ndikuyeretsa Zomwe zili 
m'mitima mwanu.Ndipo Mulungu 
Ngodziwa za mzifuwa." 1 

155. Ndithudi, mwa inu amene 
adabwerera M'mbuyo (kuthawa) 
tsiku lomwe Magulu awiri a 
nkhondo Adakumana (pankhondo 
ya Uhudi; gulu la osakhulupilira 
Ndi gulu lankhondo la Asilamu), 

1 Asilamu atagonjetsedwa choncho, gulu la adani lija lidabwerera kwawo. Koma 
ena mwa Asilamu achinyengo omwe adali m'gulu la Asilamu omwe sadathawe 
pomwe anzawo amathawa, sadakhulupirire kuti adaniwo abwerera kwawo, 
chifukwa choopa; amangoganiza kuti akadalipobe ndipo mwina awathiranso 
nkhondo kachiwiri. Tero adadzazidwa mantha m'mitima mwawo ndipo tulo 
tidawasowa. Koma Asilamu enieni sadalabadire chilichonse. Amangodya ndi 
kugona ngati kuti zopweteka sizinawakhudze. 






&#$&. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



148 



i *>» 



T JIj-*p JT 5jj-*» 






Satana ndiyemwe adawaterezetsa 
Chifukwa cha zina (Zolakwa) 
Zomwe adachita; ndipo Mulungu 
(Tsopano) wawakhululukira. 
Ndithudi, Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri, Ngoleza koposa. 

156. "E inuamene 
mwakhulupirira! Musakhale ngati 
amene sadakhulupirire, Nanena za 
anzawo pamene Akuyenda 
padziko kapena Pomwe 
akumenyana nkhondo (Ndikufera 
konko) "Akadakhala ndiife 
sakadafa, ndiponso 
Sakadaphedwa". (Mulungu 
adawathira Maganizo amenewa) 
kuti iwo akhale Chodandaulitsa 
m'mitima mwawo. Komatu 
Mulungu ndi amene Amapereka 
moyo ndi imfa. Ndipo Mulungu 
akuona Zonse zomwe Mukuchita. 1 

157. Ndipo ngati mwaphedwa 
panjira ya Mulungu, Kapena kufa, 
(palibe chotaika kwa inu) Pakuti 
chikhululuko ndi mtendere 
wochokera Kwa Mulungu 
ngwabwino kuposa zomwe 
Akuzisonkhanitsa (pamoyo 
wapadziko lapansi). 



(Ndime 156-7) Apa Asilamu akuwapepesa kuti asaganizire kuti imfayo 
yawapeza chifukwa chopita kunkhondo nkuti akadapanda kupitako sakadafa. 
Koma akuwauza kuti adafa chifukwa nthawi yawo yamoyo idatha, yomwe 
Mulungu adawalembera kuti akhale padziko lapansi. Ndipo ngakhale akadakhala 
m'nyumba zawo imfa ikadawapezabe. Ndipo akuwauzanso kuti imfa yofera 
kunkhondo yoyera njabwino kuposa yofera pakhomo. 






S 9 } • 9 * 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



149 



i *>» 



V ti\y>* JT ijj~> 



158.Ndipo ngati mumwalira 
kapena Kuphedwa, 
n'chimodzimodzi, Nonsenu) 
mudzasonkhanitsidwa Kwa 
Mulungu. 

159. Chifukwa cha chifundo 
chochokera kwa Mulungu, uli 
woleza mtima kwa iwo, (iwe 
Mtumiki Muhammad { SAW } ) . 
Ndipo Ukadakhala waukali, 
wouma mtima, ndithudi, 
Akadakuthawa. Choncho 
akhululukire ndi Kuwapemphera 
Chikhululuko (Kwa Mulungu); 
ndipo chita nawo Upo pazinthu. 
Ndipo ngati watsimikiza, tsamira 
Kwa Mulungu (basi, ndi kuchita 
chimene Watsimikiza kuchichita). 
Ndithudi, Mulungu Amakonda 
oyadzamira kwake (odalira lye). 

160. Ngati Mulungu 
akupulumutsani, Palibe amene 
angathe kukugonjetsani. Ndipo 
ngati akulekani, ndaninso 
Angakupulumutseni pambuyo 
Pokulekani. Choncho, Asilamu 
Ayadzamire kwa Mulungu basi. 

161. Nkosatheka kwa Mtumiki 
Kuchita chinyengo. Ndipo Amene 
achite chinyengo adzadza Pa tsiku 
lachimaliziro ndi zomwe 
Adazichitira chinyengo. Kenako 
Munthu aliyense adzalipidwa 
(mokwanira) Pazomwe adachita. 
Ndipo sadzaponderezedwa. 



%Sl&#A$MZ&$ 



e<3B2hSAai 






>• 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



150 



t *>» 



T ti\j*& JT 5jj^* 



162.Kodi amene akutsata 
chokondweretsa Mulungu 
angalingane ndi yemwe 
Wabwerera ndi mkwiyo 
wochokera kwa Mulungu, ndipo 
Jahanama nkukhala Malo ake? 
Taonani kuipa Kumaio obwerera! 

163. Iwo ali ndi maulemerero 
(Osiyanasiyana) kwa Mulungu. 
Ndipo Mulungu akuona zonse 
Zomwe akuchita. 

164.Ndithudi, Mulungu 
adawachitira ubwino Waukulu 
Asilamu powatumizira Mtumiki 
Wochokera mwaiwo yemwe 
akuwawerengera ma Aya ake 
(ndime zake) ndikuwayeretsa 
Ndikuwaphunzitsa Buku ndi 
(mawu a) nzeru. Ndithudi, kale 
adali mkusokera koonekera. 1 

165.Pamene sautso 
lidakupezani lomwe Inu 
mudawathira nalo (adani anu) 
Lochulukirapo kawiri, mudanena: 
"Lachokera Kuti (sautso) ili?" 
Nena: "Ilo lachokera Kwainu eni 
(chifukwa chakunyoza lamulo 
Lomwe adakuuzani). Ndithudi, 
Mulungu Ngokhoza chilichonse." 

166. Ndipo sautso lomwe 
lidakupezani tsiku Lomwe 















Apa Mulungu akukumbutsa Asilamu zachisomo chomwe adawapatsa 
pakuwapatsa Mtumiki pomwe Mtumikiyo asanawadzere iwo adali anthu osokera. 
Koma kupyolera mwa Mtumikiyo akhala olungama. 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 151 * *>» 



T OIjaP JT 5jj-k 



adakumana magulu awiri 
ankhondo, Lidali mwachilolezo 
cha Mulungu ndi kutinso 
Awaonetsere poyera okhulupirira. 

167.Ndikuwadziwitsa amene 
adachita chiphamaso 
(Amunafikina). Iwo adauzidwa: 
"Bwerani, Menyani (nkhondo) 
panjira ya Mulungu Kapena 
mwatsekereze (adani kwa ife)" 
Adati: "Tikadadziwa kuti pali 
kumenyana, Ndithudi, 
tikadakutsatani (koma kumeneko 
Kuli kuphedwa kokhakokha basi)." 
Iwo Tsiku limenelo adali pafupi 
ndikusakhulupirira Kuposa 
chikhulupiriro (ngakhale kuti 
Masiku onse amasonyeza 
Chisilamu mwachiphaMaso). 
Akunena ndimilomo yawo zomwe 
sizili M'mitima mwawo. Koma 
Mulungu akudziwa Bwinobwino 
(zonse) zomwe akubisa. 

168. Iwo ndi amene adanena za 
Abale awo (pomwe iwo) Adakhala 
osapita kunkhondo: 
"Akadatimvera, sibwenzi 
ataphedwa." Nena: "Dzichotsereni 
imfa (nokha, kuti Musafe) ngati 
mukunenadi zoona." 

169. Ndipo musawaganizire 
omwe Adaphedwa panjira ya 
Mulungu Kuti ndi akufa, koma iwo 
Ngamoyo, akudyetsedwa Kwa 
Mbuye wawo; 



*&£&&&& 












Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



152 



i *>1 



Y" Olj*P JT »}y> 









170. Akukondwera pazimene 
wawapatsa Mulungu kuchokera 
m'zaufulu Zake. Ndipo akufunira 
mafuno abwino Amene 
sadakumane nawo omwe Ali 
pambuyo pawo, (omwe alipobe 
Padziko lapansi) ponena kuti pa 
iwo Sipadzakhala mantha kapena 
kudandaula. 

171. Akukondwera chisomo ndi 
ubwino Wochokera kwa Mulungu, 
Ndi kuti Mulungu sasokoneza 
Malipiro a okhulupirira. 

172. (A wa ndi) amene 
adavomera Mulungu Ndi Mtumiki 
pambuyo povulazidwa; Kwa 
amene achita zabwino mwaiwo 
Ndikuopa Mulungu, adzakhala Ndi 
malipiro aakulu. 1 

173. Omwenso adaudzidwa ndi 
anthu (olembedwa Ganyu ndi 
Akafiri aku Makka) kuti: "Anthu 
Akusonkhanirani. Choncho 
aopeni." Koma (Zonenazo) 
zidawaonjezera chikhulupiriro 
(Asilamu). Ndipo adati: "Mulungu 
akutikwanira, Ndipo lye ndi 
mtetezi wabwino koposa." 



Asilamu makumi asanu ndi awiri (70) ataphedwa ndi enanso ochuluka 
atavulazidwa pankhondo ija ya Uhudi, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale 
naye) adawalamula Asilamu pompo, uku ali ndimabalawo, kuti awatsate adaniwo. 
Ndipo adawatsatadi. 

Koma adaniwo atamva mphekesera kuti akuwatsata naganiza kuti akutsatidwa 
ndi chigulu chankhondo cha Asilamu chachikulu, osati gulu lonlija lomwe 
adaligonjetsa. Choncho adaliyatsa liwiro kuthawa. Ndipo Asilamuwo adabwerera 
pambuyo poyenda mtunda wautali kuwatsata adaniwo. Tero Mulungu 
adawatamanda Asilamuwa pakumvera kwawo kumeneko. 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



153 t >>> 



T &\y>* JT Ijy* 



174. Choncho adabwerera 
ndichisomo Ndi ubwino 
wochokera kwa Mulungu. 
Sichidawakhudze choipa 
chilichonse; Adatsatira 
zokondweretsa Mulungu. Ndipo 
Mulungu ndimwini Ubwino 
waukulu. 

175.Ndithudiuyo 
(anakuopsezani) Ndi Satana 
yemwe amaopseza anzake. 
Choncho musawaope, ndiopeni Ine 
ngati inu mulidi okhulupirira. 

176. Ndipo asakudandaulitse 
omwe Akuthamangira kuchita 
zinthu Zachikunja. Ndithu, iwo 
Sangapereke sautso lililonse Kwa 
Mulungu. Mulungu akufuna Kuti 
asawaikire gawo lililonse La 
(zabwino) tsiku lomaliza, Ndipo 
paiwo padzakhala Chilango 
chachikulu. 

177.Ndithudi, amene 
asinthanitsa Kusakhulupirira ndi 
chikhulupiriro, Sangathe 
kumvutitsa Mulungu 
Ndichilichonse. Ndipo paiwo 
padzakhala Chilango chopweteka. 

178. Ndipo amene 
sadakhulupirire asaganize Kuti 
nthawi yaitali imene tikuwapatsayi 
Njabwino kwaiwo. Ndithudi, 
tikuwapatsa Nthawiyi kuti 
aonjezere kuchita Uchimo. Ndipo 


















Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



154 



i *>» 



T OI^aP JT ojj«* 






paiwo padzakhala Chilango 
chosambula. 

179.Nkosatheka kwa Mulungu 
Kusiya okhulupirira Momwe 
mulilimu, mpaka Atalekanitsa 
(Pakatipawo) oipaNdi abwino. 
Ndipo Nkosatheka kwa Mulungu 
Kukudziwitsani zinthu Zamseri, 
koma Mulungu Amasankha mwa 
Atumiki ake amene wamfuna 
(Nkumdziwitsa zina 
mwazimenezo). Choncho 
khulupirirani Mulungu Ndi 
Atumiki ake. Ndipo ngati 
Mukhulupirira ndi Kuopa 
(Mulungu), Painu padzakhala 
malipiro akulu. 1 

180. Ndipo asaganize amene 
akuchitira Umbombo zimene 
Mulungu awapatsa Kuchokera 
m'zaufulu Zake kuti kutero 
ndibwino Kwa iwo koma kutero 
nkoipa Kwa iwo. Adzanjatidwa 
magoli Pazomwe adazichitira 
umbombo Pa tsiku lachimaliziro. 
Ndipo Um'lowam'malo wa 
zakumwamba Ndi pansi ngwa 
Mulungu. Ndipo Mulungu 
akudziwa zonse Zimene 
mukuchita. 



Pazoopsa ndi pamene pamadziwika Msilamu weniweni. Ndipamenenso 
pamadziwikira Msilamu wachinyengo. 

2 Apa Mulungu akuchenjeza mbombo kuti zisaone kutsekemera umbombo 
wawowo. Chuma akuchichitira umbombocho chidzasanduka njoka zomwe 
zidzawazunza kwambiri. 






Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 155 * *>» 



V Otj^P JT 5jj~a 









181.Ndithu Mulungu wamva 
liwu (lonyogodola) La omwe 
(Ayuda) anena kuti: "Mulungu 
Ngosauka, ndipo Ife ndife 
olemera." Tazilemba Zimene 
anena, ndipo (talembanso) Kupha 
kwawo aneneri popanda Choonadi. 
Ndipo tidzawauza (Tsiku 
lachiweruzo): "Lawani chilango 
Chamoto owotcha." 1 

182. "Izi nchifukwa cha zomwe 
Manja anu adatsogoza. Ndithudi, 
Mulungu Sali Opondereza akapolo 
ake." 2 

183.Amene anenanso: 
"Mulungu Adatilamula ife kuti 
tisakhulupirire Mtumiki aliyense 
mpaka atabwera Ndi nsembe 
yopserezedwa ndi Moto." Nena: 
"Adakudzerani atumiki 
Ndisanadze ndi zisonyezo zooneka 
Ndi chimene mukunenachi. Nanga 
bwanji Mudawapha, ngati 
mukunenadi zoona?" 3 

184. Ndipo ngati akutsutsa iwe 
(Mtumiki Muhammad {SAW}, 

1 Ayuda adali kuchitira zamwano Mtumiki akamawalimbikitsa olemera kuti 
adzithandiza osauka. Ankati: "Kodi Mulungu wasauka tsopano kuti ife ndife 
tidzimdyetsera zolengedwa zake?" Taonani momwe adali kumchitira zamwano 
Mulungu! 

2 Awa ndi ena mwamawu omwe adzauzidwa akadzaponyedwa kumoto. 

3 Ayuda pamene Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) amawauza kuti 
amtsate amanena kuti, "Ife sadatilamule kutsata Mtumiki yemwe akuloleza anthu 
kumadya sadaka. Koma atilamula kutsata atumiki okhawo omwe akulamula kuti 
sadaka zonse azisonkhanitse pamodzi kenako azitenthe ndimoto. Kapena moto 
udze kudzapsereza." Zoonadi, atumiki otero adadza koma sadawatsate monga 
momwe Mulungu wanenera apa. Komabe sanawalamule kutsata atumiki otero 
okhawo. Kutero nkungofuna kupeza chonamizira basi. 



'»- > *l ty »{ 






Siirat 3. Al-'Imran Juzu 4 



156 



i *>» 



T ti\y>e JT 5jj**» 



M*$$k'&®& 



e. 



*jij 






sichachilendo) Adatsutsidwanso 
atumiki patsogolo pako omwe 
Adadza ndi zisonyezo zoonekera 
ndi mabuku Anzeru, ndi 
mabukunso ounika. 

185. Munthu aliyense 
adzalawa imfa. Ndithudi, 
mudzalipidwa malipiro Anu tsiku 
lachimaliziro. Ndipo amene 
adzatalikitsidwe ndi moto 
Nalowetsedwa ku Munda 
Wamtendere, Ndiye kuti 
wapambana, (kupambana 
Kwakukulu), ndipo moyo uno 
wapadziko Lapansi (sulikanthu 
koma) Ndichisangalalo chonyenga 
basi. 1 

186.Ndithu mudzayesedwa 
m'chuma Chanu ndi miyoyo yanu; 
ndipo mudzamva Masautso ambiri 
kuchokera kwa omwe 
Adapatsidwa mabuku kale 
ndiponso Kuchokera kwa omwe 
Akuphatikiza Mulungu (ndi zinthu 
Zina; Arab) koma ngati mupirira 
Ndi kudzisunga kuzomwe 
Mwaletsedwa ndi Mulungu, 
(Ndiye kuti mwachita chinthu 
chabwino Kwambiri) pakuti zinthu 
izi ndi zinthu (Zazikulu) zofunika 
munthu Kuikirapo mtima. 

187. Ndipo (akumbutse) 
pamene Mulungu adamanga 

1 Apa anthu akuwauza kuti achite zinthu molimbika zinthu zokawalowetsa 
Kumunda Wamtendere ndi kupewa kuchita zinthu, zokawalowetsa kumoto. 
Chifukwa anthu akaponyedwa kumoto kupyolera m'zochita zawo zoipa. 






J&i^d&j&i&fcJJ 



Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 



157 



i f.jir\ V OIj^p JT 5jj^ 



Chipangano ndi amene 
adapatsidwa Mabuku 
(ndikuwauza) kuti ndithudi 
Mudzalifotokoze 
mwatsatanetsatane (Bukulo) Kwa 
anthu, ndipo musadzalibise. Koma 
Adaliponya kumbuyo kwa Misana 
yawo Naligulitsa ndi mtengo 
wochepa. Taonani kuipa Chimene 
adagula (chimene adasankha)! 

188. Musaganize kuti amene 
akukondwera Zinthu (zoipa) 
zomwe achita nakonda 
Kutamandidwa ndi zomwe 
sadachite, Musawaganizire kuti 
akapulumuka Kuchilango. (Koma 
kuti) paiwo Padzakhala chilango 
chopweteka. 

189. Ndipo ufumu 
wakumwamba Ndi pansi ngwa 
Mulungu; Ndipo Mulungu 
ngokhoza Chilichonse. 

190. Ndithudi, mkalengedwe 
Kakumwamba ndi Dziko lapansi 
ndi Kusinthana kwa usiku Ndi 
usana, muli zisonyezo Kwa eni 
nzeru, 

191. Omwe amakumbukira 
Mulungu, AH chiimire ali 
chikhalire, Ndi ali chigonere 
chamnthiti Mwawo; amalingalira 
kalengedwe Ka thambo ndi nthaka 
(m'mene Mulungu adazilengera, 
uku akuti): "Mbuye wathu! 












Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 158 * *>» 1" 0^ JT Sj^ 



simunalenge Izi mwachabe. 
Ulemerero ngwanu. Tichinjirizeni 
kuchilango chamoto." 

192. "E Mbuye wathu! 
Ndithudi, Yemwe 
mudzamulowetse kumoto Ndiye 
kuti mwamuyalutsa, ndipo 
Sipadzakhala athandizi Kwa ochita 
zoipa." 

193. "Mbuye wathu"! Ndithudi, 
Ife tamva woitana Akuitanira ku 
Chikhulupiriro kuti, "Khulupirirani 
Mbuye wanu", ndipo 
Takhulupirira. E Mbuye Wathu! 
Tikhululukireni machimo athu ndi 
Kutifafanizira zoipa zathu, ndipo 
mutenge Mizimu yathu tili 
pamodzi Ndi anthu abwino. 

194. E! Mbuye wathu! 
Tipatseni Zimene mudatilonjeza 
Kupyolera mwa atumiki anu Ndipo 
musazatisambule tsiku 
lachimaliziro. Ndithudi, inu 
simuswa lonjezo. 

195. Choncho Mbuye wawo 
adawavomereza (Zopempha zawo 
ponena kuti): "Ndithudi, Ine 
Sindidzasokoneza khama 
(lantchito yabwino) Kwa ochita 
khama mwainu, kaya atakhala 
Mwamuna Kapena mkazi, (pakuti) 
inu ndinu Amodzi. Choncho 
amene asamuka (kumidzi Yawo 
mwachifuniro chawo), 



-7 















Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 159 * *>» 



Y d\ytS> JT 8jj-u 



naapirikitsidwa Midzi yawo 
navutitsidwa panjira yanga, 
Namenya (nkhondo) ndikuphedwa, 
Ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa 
Zawo. Ndipo ndidzawalowetsa 
M'minda yomwe pansi pake ndi 
patsogolo Mitsinje ikuyenda. 
Amenewo ndimalipiro Ochokera 
kwa Mulungu, ndipo kwa 
Mulungu kuli malipiro abwino." 

196.Ndithu, kusakunyenge 
Kuyendayenda padziko Kwa 
amene sadakhulupirire. 

197.Ndichisangalalo chochepa; 
Kenako malo awo ndikumoto Wa 
Jahanama. Taonani kuipa kwa 
Malo okhazikika. 

198. Koma amene aopa Mbuye 
wawo Potsatira zolamulidwa ndi 
kuleka Zoletsedwa adzapeza 
minda yamtendere Momwe 
mitsinje ikuyenda pansi ndi 
patsogolo Pake. Adzakhala 
m'menemo muyaya, Ndi phwando 
lochokera kwa Mulungu. Ndipo 
zomwe zili kwaMulungu nzabwino 
Kwa anthu abwino (kuposa 
Zosangalatsa zadziko lapansi). 

199, Ndithudi mwa amene 
adapatsidwa Buku, alipo Amene 
akukhulupirira Mulungu ndi 
zimene Zavumbulutsidwa kwa inu, 
ndi zimene Zidavumbulutsidwa 
kwa iwo, uku Akuzichepetsa kwa 



^u^&ty^i^ 



© 



"k\i 



vl/w 



5? 









Surat 3. Al-'Imran Juzu 4 160 * *>* 



V OIj^p JT 3jj-g 



Mulungu; sagulitsa ndime Za 
Mulungu ndi mtengo wochepa 
(wapadziko Lapansi). Iwo 
adzalandira malipiro awo kwa 
Mbuye wawo. Ndithudi, Mulungu 
Ngwachangu pakuwerengera. 

200. E inu amene 
mwakhulupirira! Pirirani, ndipo 
Agonjetseni adani anu 
ndikupirirako; ndipo Tetezani 
malire anu ndipo muopeni 
Mulungu kuti Mukhale opambana. 



i>9 *" * V^f'^f 'F\ *lL*f , l~f*'"£ 






\3J&3$J?o\ &\Q$\$$& 



hi^j&MjfrftM 



'ua 




Surat 4. An-Nisa' Juzu 4 161 t *>t 



t *L*Jl 5jj-*» 



Surat An-Nisa' IV 



" " ."" """ '" . r^- 

mm . 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. E inu anthu! Opani Mbuye 
wanu yemwe Adakulengani 
kuchokera mwa munthu Mmodzi 
(Adam) ndipo adalenga mmenemo 
Mkazi wake (Hawa), ndipo 
adafalitsa amuna ndi Akazi ambiri 
kuchokera mwa awiriwo. Ndipo 
opani Mulungu yemwe kupyolera 
Mwa lye mumapemphana. Ndipo 
(sungani) chibale. Ndithudi 
Mulungu ndimyang'aniri pa inu 
(Akuona chilichonse chimene 
muchita). 1 

2. Ndipo apatseni ana amasiye 
chuma chawo; Musasinthanitse 
choipa ndi chabwino. (Musasankhe 
choletsedwa); ndipo musadye 
Chuma chawo pochiphatikiza ndi 
chuma chanu. Ndithudi, (zonsezo) 
ndiuchimo waukulu. 



o&£\<£&\&\j 









Ndime iyi ikulimbikitsa zakuopa Mulungu ndi kumulemekeza potsatira 
malamulo ake ndi kupewa zomwe lye waletsa. lye ndi amene adakulenga. 
Ndiyemwenso adalenga zonsezimene iwe adakulengera. Ngakhale iwe 
amene utafuna chithandizo kwa anzako umampempha ponena kuti 
"Ndikukupempha m'dzina la Mulungu kuti undichitire chakuti." Izi umachita 
poona kuti iye adzalemekeza dzina la Mulungu, ndipo adzakwaniritsa chomwe 
ukufunacho. Koma nanga bwanji ukuchita zimene Mulungu waletsa? Bwanji 
sukulemekeza lamulo lake pomwe iwe ukufuna kuti anthu achite zomwe 
sukuchita. Apa akutiuzanso kuti Mulungu akuona chilichonse chimene anthu 
ake akuchita, ngakhale chikhale chochepa chotani. 



Surat4. An-Nisa 9 Juzu 4 



162 



t *>t 



t *L-jJt *JJ-" 






3. Ngati mwaopa kuti 
simungachite chilungamo Pa 
amasiye (opaninso kusawachitira 
Chilungamo akazi pamitala), 
choncho Kwatirani amene 
mukuwafuna mwa akazi; Awiri, 
kapena atatu, kapena anayi (basi). 
Koma ngati mukuopa kuti 
simungathe kuchita Chilungamo, 
(kwatirani) mmodzi basi kapena 
Amene manja anu akumanja 
adapeza (mdzakazi). Kutero 
kudzakuchititsani kuti 
musapendekere (Kumbali 
yosalungama). 1 



1 Maulama onse a Malamulo a Chisilamu adamvana kuti ndime iyi yaika 
malire amitala yomwe munthu akhoza kukwatira. Ndipo ikuletsa kukwatira 
akazi opyola anayi panthawi imodzi. Naonso mahadisi a Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) akuthirira ndemanga nkhani yokhayokhayi. 
Kwanenedwa kuti "Ghayilan", mkulu wina waku Taif adali ndi akazi asanu ndi 
anayi (9). Ndipo pamene analowa m'Chisilamu mtumiki anamuuza kuti atsale 
ndi akazi anayi okha. Enawo awasudzule. Ndipo palinso nkhani ya Naufali 
Bun Muawiya yemwe atalowa m'Chisilamu Mtumiki adamulamula kuti pa 
akazi ake asanu asudzulepo mmodzi kuti atsale ndi anayi, Koma ngakhale zili 
choncho pafunika kuiganizira mozama ndime imeneyi pamene ikumloleza 
munthu kukwatira akazi opyolera mmodzi. Nkofunika kuti akazi onsewo 
awachitire zachilungamo powagawira zofuna zawo mofanana popanda 
kukondera aliyense waiwo. Tero, munthu akachita chilolezochi mwachabe 
nakwatira mitala popanda kuchita chilungamo pakati pawo ndiye kuti 
akuchitira Mulungu chinyengo. Pachifukwa ichi, mabwalo a Chisilamu 
ozengera milandu apatsidwa mphamvu yokakamizira anthu kuti achite 
chilungamo pamitala kuti chomwe mkazi sadamchitire, amchitire. Koma 
ngakhale zili choncho ndikulakwa kwakukulu kuganizira kuti chilungamo 
chomwe chaikidwacho chikuchotsa chilolezo chokwatira mitala. Umo 
simmene Qur'an ikunenera, iyayi. Asilamu omwe ali ndimaganizo amenewa 
ndiomwe amira m'maganizo a Akhrisitu a ku Zambwe. Asilamuwa amati 
"Nayonso Qur'an ikuletsa kukwatira mitala. Koma kuti siinachotse 
mwamtheradi lamulo lakukwatira mitala chifukwa chakuti idaona kuti chidali 
chinthu chanzeru kutero panthawiyo poti chizolowezi chamitalachi chidafala 
ponseponse. Tero, mmalo mwake idaloleza anthu kukwatira mitala ngati 
angawachitire akazi awowo zachilungamo. Tsono poti chilungamochi nkovuta 
kuchikwaniritsa pamitala, chimene chilipo apa nkuti pasakhale mitala." 



Surat4. An-Nisa' Juzu 4 



163 



£ *>i 



t *L*Jl Sjj-** 



4. Ndipo akazi apatseni mahari 
Awo (chiwongo) monga mphatso. 
Koma (akazi anuwo) ngati 
Atakupatsani mokoma mtima 
Chilichonse (M'chiwongocho), 
Idyani mokondwa ndi 
Mothandizika nacho. 1 

5. Ozerezeka musawapatse 
chuma chanu Chomwe Mulungu 
wachichita kukhala Cholimbitsa 
matupi anu ndi moyo wanu. Koma 
adyetseni nacho ndikuwaveka 
nacho Ndikuwauza mawu abwino 
(Monga kuti: Mukadzakula 
Ndikukhala olungama, 
Tidzakupatsani chuma chanu). 2 









Ndithudi, maganizo amenewa ngodabwitsa poona momwe Asilamu ena 
akugonjera zonena za Akhrisitu. Chifukwatu kukwatira mitala sichinthu choipa. 
Mwina kutero kungakhale kofunika zedi kwa anthu ena kuti kuwaletse 
kulumpha malire a Mulungu. Pali anthu ena amene ali ndi mphamvu zambiri 
zachibadwa omwe sangakhutitsidwe kukhala ndimkazi mmodzi. Chilolezo 
chokwatira mitala mpaka kulekeza pa akazi anayi chimawapewetsa anthu 
monga awa kumachitidwe achiwerewere. Qur'an ikuloleza anthu monga 
amenewa kukwatira mitala ngati angachite chilungamo. Koma amene akuti 
kukwatira mitala nkoipa, akufuna kungotsutsana ndi Qur'an. 

1 Kumuitanitsa chiwongo mkazi wako chimene udampatsa kapena kumlipitsa 
ndalama iliyonse, zotere nzosaloledwa.Koma ngati iye mwini atakugawira 
mokoma mtima kachinthu kam'chiwongocho landira usamkanire. Monga iwe 
umampatsa, iyenso akhoza kukupatsa. 

2 Ayang'aniri a ana amasiye, monga momwe awauzira kuti asawachenjerere 
ana amasiye koma kuti awapatse chuma chawo mokwanira, apa 
akuwauzanso kuti apitirize kuyang'anira chuma cha ana amasiyewo. 
Asawapatse pomwe sali ozindikira zinthu, ali ofooka m'maganizo pomwe 
sakuzindikira kufunika kwachuma kuopa kuti angaononge chumacho 
mosalongosoka. Tero asawapatse ngakhale misinkhu yawo ili yaikulu. Koma 
apitirize kuwasungira chumacho ndi kumawauza mawu abwino ponena kuti 
"Mpaka pano ndikuona kuti mwanokha simungathe kuchiyendetsa bwino 
chuma chanu. Tero ndiloleni ndikusungirenibe mpaka nthawi yochepa 
kutsogoloku. Ndikadzaona kuti nzeru zakhazikika apo mpomwe 
ndidzakupatsani chumachi. Chifukwa chakuti chuma chamwana wamasiye 
chitaonongeka, kulakwa kwake sikudzakhala kwa wamasiye yekhayo. Koma 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 4 



164 



i tj*-i 



t *l*Ji djj-** 



6. Ayeseni amasiye 
(akayandikira kukula Msinkhu kuti 
muone kuti atha kuchita ntchito 
Yabwino ndi chuma chawo 
mukawapatsa) Kufikira atafika 
nthawi yokwatira/kukwatiwa. 
Ndipo ngati mutawaona kuti ali 
ndi nzeru zabwino, Apatseni 
chuma chawo. Musachidye 
mosasamala Ndi mwachangu 
poopa kuti angakule. Ndipo 
Amene ali opeza bwino adziletse 
(kulandira Mphoto yolerera ana 
amasiyewo). Koma amene Ali 
wosauka adye mwaubwino (osati 
Moononga). Ndipo pamene 
mukuwapatsa chuma Chawo, 
funani mboni (zoonerera 
kuperekedwa Kwa chumacho). 
Ndipo Mulungu ali Wokwana 
Kukhala Muwelengeri (ndi 
Woyang'anira). 1 

7. Amuna m ' chuma chimene 
makolo ndi achibale Asiya ali ndi 
gawo. Naonso akazi ali ndigawo 
M' chuma chimene asiya makolo 
ndi achibale (Chapafupi), ngakhale 
chitakhala chochepa Kapena 
chochuluka ndigawo Logawidwa 
(ndi Mulungu). 









kudzakhudzanso munthu wosungawe. Chumatu ndicho chinthu chokonzera 
zinthu zambiri, zabwino. Tero nkofunika kuti chisamalidwe. 

1 Komatu akhale akumuyesayesa wamasiyeyo pomusiira kuti nthawi zina 
aziyendetsapo yekha chumacho kuti aphunzire kasamalidwe kake. Akaona 
kuti akukhoza, ampatse Asamachedwetsere mwadala. 

2 Apa tsopano akufotokoza mmene chuma chamasiye angachigawire ponena 
kuti m'Chisilamu akazi akuwalola kuwagawirako chuma cha abale awo, osati 



Surat4. An-Nisa' Juzu 4 



165 



t *>t 



t 5-L-Jl 5jj-»» 



8. Ndipo panthawi yogawa 
Akadza achibale, amasiye Ndi 
osauka (omwe alibe Gawo 
pachumacho), apatseniko Kanthu 
ndi kunena nawo mawu abwino. 1 

9. Ndipo (wowasiirawo) aope 
kuchenjerera Amasiye, kuti naonso 
ngati atasiya ana awo Ofooka 
pambuyo, akadawaopera (kutaika). 
Choncho aope Mulungu ndipo 
anene mawu Olingana (kwa ana 
amasiye wo). 

10. Ndithu, amene akudya 
chuma cha Ana amasiye 
Mopondereza, Akudya ndi kuthira 
moto M'mimba zawo. Ndipo 
Adzalowa kumoto woyaka! 

11. Mulungu akukulamulani za 
ana anu achimuna Apate gawo 
lolingana ndi gawo la akazi Awiri. 
Ngati akaziwo ali (opitirira) awiri, 
Ndiye kuti adzalandira Zigawo 









kuti amuna okha ndiwo, owagawira. Koma gawo lomwe mkazi amapatsidwa 
limacheperapo poyerekeza ndi gawo lomwe mwamuna amalandira. Chifukwa 
chakuti mwamuna ndiye ali ndi udindo waukulu poyerekeza ndi mkazi. 
Mwamuna ali ndi udindo woyang'anira mkazi wake, ana ake ndi makolo ake. 
Koma mkazi alibe udindo woyang'anira mwamuna wake. Ndiponso alibe 
udindo woyang'anira mwana kapena makolo ake, pokhapokha ngati tate wa 
anawo ali wochepa nzeru. Zikatero mpomwe mkaziyo amakhala ndi udindo 
woyang'anira ana ake. Ndipo udindo wamkazi poyang'anira makolo ake uli 
wochepa (theka) poyerekeza ndi mlongo wake. 

1 Chuma nchinthu chimene chimachotsa moyo wamunthu mmalomwake, 
makamaka ngati chikupezeka m'njira yaulere yosachivutikira, monga chilili 
chuma chamasiye. Choncho amene alibepo gawo pachumacho amangoti diso 
tong'o, kusirira. Ndipo nchifukwa chake Mulungu apa akunena kuti pogawa 
chuma chamasiyecho ngati achibale atabwerapo omwe alibepo gawo 
pachumacho, awapatseko kachinthu kochepa ndi kuwapepesa kuti chomwe 
awapatsacho nchochepa. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 4 



166 



i frjJrl 



t ^L— ui ^JJ- 4 



ziwiri mwazigawo zitatu (%) za 
(Chumacho) chimene wasiya 
(womwalira), Ngati Mwana 
wamkazi ndi mmodzi, apatsidwe 
Chigawo chimodzi mwa zigawo 
ziwiri (Y 2 ) Naonso makolo ake 
awiri aliyense waiwo Alandile 
chigawo chimodzi mwazigawo 
zisanu Ndi chimodzi (V 6 ) 
chachuma chosiidwacho, ngati 
(Womwalirayo) wasiya mwana 
(kapena Mdzukulu). Koma ngati 
sadasiye mwana, ndipo Makolo 
ake awiri ndiwo awasiira, ndiye 
kuti Mayi wake alandire chigawo 
chimodzi Mwazigawo zitatu QA) 
chachumacho, (ndipo Bambo 
alandire ( 2 A). Ngati wakufayo 
wasiya Abale, ndiye kuti mayi 
Wake apeza chigawo chimodzi 
mwazigawo Zisanu ndi chimodzi 
(V 6 ) chachumacho. (Kugawa 
Chumaku kuchitike) atachotsapo 
chimene iye Adalamulira kuti 
adzachipereke kwakutikwakuti, 
Kapena kulipira ngongole (zake). 
Atate anu ndi Ana anu, simudziwa 
inu kuti ndani mwaiwo Amene ali 
ndi chithandizo chapafupi kwainu. 
Amenewa ndi malamulo omwe 
akhazikitsidwa Ndi Mulungu. 
Ndithudi, Mulungu Ngodziwa 
Kwambiri, Ngwanzeru zakuya. 1 






1 Apa akufotokoza zakagawidwe kachuma chamasiye (mirath). 

a) Ngati munthu wamwalira nkusiya, ana amuna ndi akazi tero mwana 

wamwamuna adzapeza magawo awiri ndipo wamkazi adzapeza gawo limodzi. 



Siirat4. An-Nisa' Juzu 4 



167 



i *>» 



t tL— Jl $jj-*» 



12. Inunso mupata chigawo 
chimodzi mwazigawo Ziwiri (Vi) 
chachuma chimene akazi anu 
Asiya ngati alibe mwana (kapena 
mdzukulu) ngati asiya Mwana 
ndiye kuti inu mupata chigawo 
chimodzi M'zigawo zinayi ( V4) 
chachuma chosiidwacho 
Mutachotsapo zomwe adalamula 
kuti zipite Kwakutikwakuti kapena 
ngongole zake, Naonso akazi anu 






b) Munthu akafa nkusiya ana akazi okha, awiri kapena ochulukirapo, anawo 
adzatenga magawo awiri achumacho. Ndipo onsewo alandire 
mofanana.Pasapezeke wotenga zochuluka kuposa wina. 

Tsono gawo lomwe latsala lidzaperekedwa kwa ena oti awagawire ngati alipo. 
Ngati palibe, ndiye kuti gawolo lidzaperekedwanso kwa ana akaziwo. 
N.BH Magawo awiri m'magawo atatu C 2 ^), apa akutanthauza kuti chuma 
chonsecho amachigawa m'magawo atatu ofanana. Ndipo akaziwo nkulandira 
magawo awiri mwamagawo atatuwo. 

c) Ngati munthu atamwalira nkusiya mwana mmodzi wamkazi, ndiye kuti 
chumacho achigawe magawo awiri ofanana. Gawo limodzi mwamagawo awiri 
aja alipereke kwamwana wamkaziyo. Ndipo gawo lotsalalo alipereke kwa ena 
ofunika kuwagawira ngati alipo. Ngati palibe, aliperekenso kwa mwana 
yemweyo. Lamulo la adzukulu likufanana ndilamulo la ana ngati wakufayo 
adalibe ana koma adzukulu ake okha. 

d) Munthu akafa nkusiya ana ndi makolo ake, (tate ndi mayi), tero tate 
adzapeza gawo limodzi mwamagawo asanu ndi limodzi (v 6 ) a chumacho. 
Nayenso mayi adzapeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (7*). 
Ndipo chuma chotsaliracho adzalandira ndi ana kapena adzukulu amuntnu 
wakufayo. 

e) Munthu akafa nkusiya tate wake ndi mayi wake basi, popanda ana ndi 
adzukulu choncho apa mayi adzalandira gawo limodzi mwamagawo atatu 
achumacho. Ndipo tate adzatenga magawo awiri. 

f) Munthu akafa nkusiya mayi wake yekha ndi abale ake obadwa nawo kwa 
mayi ndi bambo mmodzi, kapena akumbali yakwabambo okha kapena 
akumbali yamayi okha, apa mayi adzalandira gawo limodzi mwamagawo 
asanu ndi limodzi achumacho. Anthu oyenera kuwagawira chuma chamasiye 
asawagawire msanga chumacho mpaka ngongole zonse zawakufayo 
atazibweza. Ndiponso mpaka apereke chilawo (wasiya) chomwe wakufayo 
adanena kuti chidzachitike. Owagawira chumawo asakhale anthu osusuka 
ndichumacho. Choyamba aonetsetse kuti izi zonse zakwaniritsidwa. Komatu 
chilawocho chisapyole pagawo limodzi mwamagawo atatu (73) achumacho. 
Chikapyolera pamenepa ndiye kuti choonjezerapocho sichivomerezedwa. 



Surat 4. An-Nisa' 



Juzu 4 



168 i *>» 



t s-L-jJl 3jj~*» 



apata chigawo chimodzi 
M'zingawo zinayi ( V4) pachuma 
chomwe Mwasiya, ngati mulibe 
mwana (ndi mdzukulu). Koma 
ngati mwasiya mwana (ndi 
mdzukulu), (Akaziwo) apata 
chigawo chimodzi m'zigawo 
Zisanu ndi zitatu ( vg) pachuma 
chomwe mwasiya Mutachotsapo 
chomwe mudanena kuti chipite 
Kwakutikwakuti kapena kulipira 
ngongole (Zanu), Ngati mwamuna 
kapena mkazi Olowedwa m'malo 
pachuma pomwe alibe Mwana (ndi 
mdzukulu) ngakhale makolo awiri, 
Koma ali naye m'bale wake 
(wakuchikazi) kapena Mlongo 
wake (wakuchikazinso) aliyense 
Waiwo apata chigawo chimodzi 
m'zigawo Zisanu ndi chimodzi 
(V5). Ndipo ngati ali 
Ochulukirapo, ndiye kuti 
agawirana chigawo Chimodzi 
m'zigawo zitatu ( V3) cha 
chumacho Pambuyo pochotsapo 
chomwe chidanenedwa kuti 
Chipita kwakutikwakuti kapena 
kulipira ngongole, Popanda 
kupereka mavuto. Awa ndi 
malamulo Ofunika omwe achokera 
kwa Mulungu. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa kwambiri (pokhazikitsa 
Malamulo); Woleza (pa akapolo 
ake). 1 






1 Apa akufotokoza mmene anthu ena angawagawireko chuma chamasiye. 
a) Ngati atafa mkazi nkusiya mwamuna wake yekha popanda kusiya ana 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 4 



169 



t *>» 



£ s-L-Jl 5jj**» 



13. Amenewo ndiwo malire a 
Mulungu; (Musawalumphe). 
Ndipo amene angamvere Mulungu 
ndi Mtumiki Wake 
adzamulowetsa M'minda yomwe 
pansi ndi patsogolo pake Mitsinje 
ikuyenda. Adzakhala m'menemo 
Muyaya. Kumeneko ndiko 
kupambana Kwakukulu. 

14. Koma amene anganyoze 
Mulungu ndi Mtumiki wake, ndi 
kulumpha Malire ake, (Mulungu) 
adzamulowetsa Kumoto; 
nadzakhala m'menemo Muyaya. 









kapena adzukulu, mwamunayo alandire gawo limodzi mwamagawo awiri 
achuma ( ^l^ chomwe wasiya mkazi wakecho. 

b) Akafa mkazi nkusiya mwamuna ndi mwana wake kapena mdzukulu wake 
apa ndiye kuti mwamunayo adzalandira (7 4 ) chigawochimodzi mwazigawo 

zinayi zachumacho. 

c) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake popanda mwana kapena mdzukulu 

wake ndiye kuti mkaziyo adzalandira (7 4 ) chigawo chimodzi mwazigawo 

zinayi zachuma chamwamuna wakecho. Ndipo chotsalacho achipereke kwa 
ena ofunika kuwagawira. 

d) Akafa mwamuna nkusiya mkazi wake ndi mwana wake kapena mdzukulu 

wake, apa mkazi alandire ( 1 /q) chigawo chimodzi mwazigawo zisanu ndi 

zitatu zachuma chamwamunayo. 

e) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena zidzukulu ndi makolo, 
koma nkusiya mbale mmodzi wamwamuna kapena wamkazi wakumbali 

yamayi, apa ndiye kuti mbaleyo adzalandira ( 1 /g) gawo limodzi mwamagawo 

asanu ndi limodzi achumacho. Ndipo chotsalacho adzawagawira ena oyenera 
kuwagawira ngati alipo. Koma ngati palibe ndiye kuti mbaleyo adzatenganso 
chotsalacho. 

f) Akamwalira munthu popanda kusiya ana kapena adzukulu ndi makolo, 
koma wasiya abale akumbali yamayi, amuna kapena akazi, apa ndiye kuti 

abalewa adzalandira (V3) gawo limodzi mwamagawo atatu achuma 

chawomwalirayo. Ndipo adzagawana pakati pawo mofanana amuna ndi akazi 
omwe. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 4 



170 



t *>i 



£ tL-Jl djj^ 



Ndipo adzapeza Chilango 
chosambula. 

15. Ndipo omwe achite chauve 
(chigololo) mwa Akazi anu, 
afunireni mboni zinayi za mwainu 
Zoikira umboni paiwo. Ngati 
ataikira umboni (Kuti achitadi 
chauvecho), atsekereni M'nyumba 
kufikira imfa idzawapeze, kapena 
Mulungu adzawaikire njira ina 
(monga Kuphedwa). 1 

16. Ndipo amuna awiri mwainu 
amene akuchita Zauve (monga 
kuchitana ukwati amuna Okhaokha 
' matanyula'), akhaulitseni 
(Powavutitsa). Tsono ngati atalapa 
Ndikukonza bwino (mkhalidwe 
wawowo) Asiyeni. Ndithudi, 
Mulungu Ngolandira kulapa, 
Ndiponso Ngwachisoni chambiri. 

17. Ndithudi kulapa 
kovomerezeka ndi Mulungu 
ndikwa omwe amachita zoipa 
mwaumbuli kenako nkulapa 
mwachangu. Amenewo ndiomwe 
Mulungu Amawalandira kulapa 
kwawo. Ndipo Mulungu Ngodziwa 
Kwambiri Ngwanzeru zakuya. 2 



^4 (I# 3jys3i QaK> '($& 









1 (Ndime 15-6) Izi ndi ndime zimene zikufotokoza zazilango zolanga nazo awa> 

a) Akazi amene amachitana ukwati okhaokha 

b) Amuna amene amachitana ukwati okhaokha 

c) Akazi ndi amuna amene akuchitana ukwati pamalo achabe apathupi. Zinthu 
zonsezi nzoipa kwabasi, makamaka kuchitana ukwati amuna okhaokha ndi 
kuchitananso ukwati akazi okhaokha. 

2 Ndime iyi ikusonyeza kuti Mulungu amalandira kulapa kuchokera kwa aliyense 
amene walapa. Komatu kuti kulapako kuvomerezeke, pafunika zinthu ziwiri:- 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 4 



171 



f *>» 



t j-L— Jl 5jj-*» 



18. Kulapa sikungalandiridwe 
pa omwe Akuchita zoipa mpaka 
imfa kumfikira M'modzi waiwo 
(Pamenepo) nkunena: "Ndithudi 
ine ndikulapa tsopano." 
Ngakhalenso pa omwe akufa ali 
Osakhulupirira. Iwo tawakonzera 
Chilango chopweteka. 

19. E inu amene 
mwakhulupirira! 
Sikovomerezedwa kwainu 
kuwalowa Chokolo akazi 
mowakakamiza. Ndipo 
musawaletse (kukwatiwa Ndi 
amuna ena) ndi cholinga choti 
Muwalande zina mwa zomwe 
Mudawapatsa, (nkosaloledwa 
kutero) Kupatula ngati atachita 
choipa Choonekera. Ndipo khalani 
nawo Mwaubwino. Ngati 
mutawada (Musalekane nawo), 
mwina Mungade Chinthu chomwe 
Mulungu waika Zabwino zambiri 
mkati mwake. 1 






a) Akachita utchimo alape mwachangu. Osati azingopitiriza kulakwako mpaka 
akadzaona kuti ali pafupi kufa ndiye nkuyamba kulapa, zoterezi iyayi. 

b) Utchimowo ukhale kuti adauchita chifukwa chaumbuli. Apa tikutanthauza 
kuti panthawiyo iye adadzazidwa ndi zilakolako zauchimo ndipo zidamchititsa 
kuti achimwe. Koma osati tchimolo likhale lolichita tsiku ndi tsiku popanda 
kulabadira chilichonse. Kulapa kwa uchimo wotero Mulungu sangakulandire. 
Ndipo mmalo mwake akamulanga ndi chilango chaukali. 

1 Chisilamu chisanadze, chikhalidwe cha Arabu chidali chonchi:- Tate 
wamunthu akamwalira ana ake amamlowera chokolo akazi ake omwe 
sadabereke anawo. Mwana aliyense amalowa chokolo mwa mkazi watate 
wake yemwe sadali mayi wake wom'bala. 

a) Akafuna kumkwatira adali kumtenga. 

b) Ndipo akafuna kumkwatitsa kwa mwamuna wina, amamlamula ndalama 
mwamunayo iye natenga ndalamazo. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 4 



172 t *j*-i 



t s-LmJI 5jj-*> 



20. Ndipo ngati mufuna 
kusintha mkazi wina M'malo mwa 
wina (pokwatira wina kusiya 
Wakale) pomwe mmodzi waiwo 
(woyambayo) Mudampatsa 
milumilu yachuma, musatenge 
(Kulanda) chilichonse. Kodi 
mungachitenge Mwa chinyengo 
ndi utchimo Woonekera? 

21. Kodi mungachitenge bwanji 
Pomwe mudalowana Wina ndi 
mnzake, ndipo (Akazi) adalandira 
kwa Inu chipangano cholimba? 

22. Ndipo musakwatire akazi 
amene adakwatiwapo Ndi atate 
anu, kupatula zomwe zidapita, 
(Musabwerezenso kuzichita). 
Ndithudi, Chinthu ichi nchauve 
ndipo nchodedwa Ndiponso 
ndinjirayoipa. 1 









c) Kapena amangomuvutitsavutitsa kuti akafuna adziombole yekha pomlipira 
ndalama mwanayo. 

d) Kapena amangommanga kuti asakwatiwenso mpaka imfa yake. Choncho 
apa Mulungu akuletsa machitidwe oipawa, 

1 Ndime iyi ndi zinzake zotsatira zikufotokoza zaakazi omwe ngoletsedwa 
kuwakwatira pa Shariya ya Chisilamu. Ena mwa akaziwo ndi awa:- 

1) Munthu sangakwatire mkazi yemwe bambo wake adamkwatirapo kapena 
yemwe adakwatiwapo ndi gogo wake wakuchimuna kapena kuchikazi. Koma 
osati amene adasiidwa ndimalume ake kapena m'bale watate wake. 
Amenewa akhoza kuwakwatira. 

2) Mayi wako yemwe adakubereka ndi mayi wamayi wako. 

3) Mwana wako wodziberekera wekha, kapena mwana amene mwana wako 
adabereka. 

4) Tate wako wamkazi (zakhali) ndi alongo agogo ako. 

5) Mayi wako wamng'ono (mbale wamayi wako) ndi mbale wamkazi wa agogo 
ako akuchikazi. 

6) Mwana wambale wako wobadwa naye bambo ndi mayi mmodzi kapena 
wobadwa naye mayi mmodzi kapena bambo mmodzi ndi ana onse akazi 
oberekedwa ndi mwanayo. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



173 



*jjfc-l 



t $,L**Jl ^JJ -- 



23. Kwaletsedwa kwainu 
kukwatira Amayi anu, ana anu, 
alongo anu, Azakhali anu, amayi 
anu aang'ono Kapena aakulu, ana 
achikazi am' bale Wanu, ana 
achikazi a mlongo wanu, Amayi 
anu amene adakuyamwitsani, 
Alongo anu oberekedwa ndi amene 
adakuyamwitsanipo. Mayi a akazi 
anu, Ana achikazi owapeza amene 
Mukuwasunga woberekedwa ndi 
Akazi anu omwe mwalowana 
nawo. Koma ngati simudalowane 
nawo, Nkosaletsedwa kwa inu 
kukwatira Amayi awowo; ndi 
akazi a ana Amuna omwe 
ngochokera kumisana yanu. 
Ndiponso nkoletsedwa kwa inu 
kukwatira Mophatikiza mkazi ndi 
mchemwali wake obadwa naye 
Kupatula zomwe zidapita. 
Ndithudi Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri Ngwachisoni zedi. 

24. Ndiponso (nkoletsedwa kwa 
inu kukwatira) Akazi okwatiwa 
kupatula chimene manja anu 
akumanja apeza (mdzakazi). Hi ndi 
lamulo la Mulungu lomwe lili 
painu. Ndipo kwalolezedwa 
kwainu (kukwatira Akazi) omwe 









7) Mwana wamkazi wamlongo wako (mfumukazi) wamayi ndi bambo mmodzi 
kapena wakumbali yabambo yokha kapenanso wakumbali yamayi yokha. 

8) Mkazi yemwe adakuyamwitsapo ndi mayi ake amkaziyo kapena omwe 
adamuyamwitsaponso iye. 

9) Mkazi yemwe unayamwa naye bere limodzi. 

10) Mayi wamkazi wanu. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



174 • *>' 



i iI~jS\ Ojj— » 



sali m'gulu ili. Afunefuneni Ndi 
chuma chanu m'njira yaukwati, 
Osati chi were were. Choncho, 
amene Mwawakwatira mwa iwo 
nkusangalala nawo, apatseni 
chiwongo chawo Chomwe 
chakakamizidwa. Palibe kuipa 
Kwa inu (kupereka) chomwe 
mwagwirizana M'malo 
mwachomwe chidatchulidwa. 
Ndithudi, Mulungu Ngodziwa, 
Ngwanzeru zakuya (Pokhazikitsa 
Malamulo Ake). 

25. Ndipo amene sangathe mwa 
inu Kupeza chuma chokwatirira 
mkazi Amene ali mfulu wa 
Chisilamu, (akwatireni) Adzakazi 
achisungwana a Chisilamu, Mwa 
omwe manja anu akumanja apeza, 
Mulungu akudziwa kwambiri 
chikhulupiriro Chanu. Ndinu 
amodzi kuchokera kwa wina ndi 
mnzake (nonsenu ndinu ana a 
Adam). Akwatireni ndi chilolezo 
cha mabwana awo, Ndipo apatseni 
chiwongo chawo Mwachilamulo. 
(Akwatireni) omwe ali Akazi 
odzisunga, osati achiwerewere 
kapena ochita zibwenzi. Ndipo 
akakwatiwa, kenako nkuchita 
Chauve, chilango chawo nditheka 
lachilango cha mfulu. kumeneko 
(Kukwatira akapoloko) ndilamulo 
kwa yemwe mwa inu akuopa kuti 
angachite chi were were. Koma 









Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



175 



t,j)r\ 



£ s-L-jJl &jj-»» 



Ngati mutapirira (posiya kukwatira 
Akapolo) ndibwino kwa inu 
kutero. Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka, Ngwachisoni 
chambiri. 

26. Mulungu akufuna 
kukufotokozerani Ndi 
kukutsogolerani kunjiraZaomwe 
adalipo patsogolo Panu; ndiponso 
akufuna Kukufewetserani. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa kwambiri, 
Ngwanzeru zakuya. 

27. Ndiponso Mulungu 
Akufuna kukufewetserani. Koma 
amene akutsata zilakolako zawo 
akufuna Mupotoke; kupotoka 
kwakukulu. 

28. Mulungu akufuna 
kukupeputsirani, pakuti Munthu 
adalengedwa wofooka. (Alibe 
Mphamvu zathupi ngakhale 
zolimbana ndi Zilakolako 
zamoyo). 

29. E inu amene 
mwakhulupirira! Musadye chuma 
chanu mwachinyengo Koma 
m'njira yamalonda Ndi moyanjana 
pakati panu. Ndipo Musadziphe 
nokha (ngakhale Kupha anzanu). 
Ndithudi, Mulungu ali Wachisoni 
pa inu. l 






®, 












m,^m?* s 



*&»%$ 



1 Apa akuletsa kudyerana chuma m'njira yachinyengo. Koma kugulitsana 
malonda mwachimvano onse awiri nkomwe kukuloledwa. Ndipo Mulungu 
pomwe wanena kuti musadziphe, m'mawu amenewa mukutanthauza munthu 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



176 



o *jJH 



i $.L«Jl &jj**> 



30. Ndipo amene achite izi 
molumpha Malire ndi mopanda 
chilungamo, Iyeyo tidzamulowetsa 
kumoto. Ndipo zimenezo 
nzopepuka kwa Mulungu. 

31. Ngati mudzitalikitsa 
kumachimo Akuluakulu omwe 
mukuletsedwa, Ndiye kuti 
tikufafanizirani Zolakwa zanu 
(zing'onozing'ono) Ndipo 
tidzakulowetsani Malo aulemu. 1 

32. Ndipo musazilakelake 
(mwadumbo) Zomwe Mulungu 
wawadalitsa nazo Ena mwainu. 






j&3& 






<3> 



*i4$i&-Si*&3ji> 






kudzipha yekha, ndi kupha Msilamu mnzake poti Msilamu ndi Msilamu 

mnzake ali ngati thupi limodzi. Ndipo ngakhale yemwe sali Msilamu saloledwa 

kumupha. 

Mawu oti "kupha" akutanthauza kupha munthu nkuferatu nthawi yomweyo. 

Mawuwa akutanthauzanso kuchita chinthu chomwe chingamchititse munthu 

uja kuonongeka mwapang'onopang'ono mpaka mathero ake nkuferatu. Izi zili 

monga amene akumwa mowa wakachasu kapena wina uliwonse, akudzipha 

yekha. Kapenanso kuchita chinthu china chilichonse chomwe mathero ake 

chimamupha munthu. Ndipo nayenso amene akuthandizira zimenezi, ali 

m'gulu lakupha munthu. 

1 Apa akuti ngati tipewa machimo akuluakulu, Mulungu adzatikhululukira 

timachimo ting'onoting'ono. 

Munthu nkovuta kuupewa utchimo ung'onoung'ono. Utchimotu suli wofanana. 

Pali wina waukulu. Palinso wina wokulitsitsa. Ndipo pali waung'ono ndi wina 

wochepetsetsa. 

Machimo akuluakulu ali ngati awa: (a) Kuphatikiza Mulungu ndi mafano (b) 

Kupha munthu wosalakwa. (c) Kuba. (d) Kuchita malonda akatapira (riba) (e) 

Kumwa zoledzeretsa. ( f) Kuchita ziwerewere ndi zina zotero. 

Tsono utchimo waung'ono uli monga: Kunena mawu osafunika ndi 

kuchiyang'ana chinthu choletsedwa ndi zina zotero zomwe nzovuta munthu 

kuzipewa. Choncho, munthu akapewa machimo akuluakulu ndiye kuti 

adzamkhululukira machimo ang'onoang'ono ngati sakuwachita mochuiukitsa. 

Enanso mwamachimo akuluakulu ndikusiya kutsata malamulo a Mulungu, 

monga 

(a) Kusiya kupemphera Swala zisanu (b) Kusiya kupereka Zakati ndi 

zithandizo zina zofunika, (c) Kusiya kumanga m'mwezi wa Ramadhani, (d) 

Kusiya kuchita Haji, (e) Kusiya kuyang'anira makolo ndi zina zotero. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



177 



o *>i 



t *L*Jt *jj-*» 



Amuna ali ndi gawo (Lokwanira) 
la zomwe apeza. Nawonso Akazi 
ali ndi gawo(lokwanira) la Zomwe 
apeza. Ndipo mpempheni Mulungu 
zabwino zake. Ndithudi, Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 1 

33. Ndipo anthu tawaikira 
alowa Mmalo pazomwe asiya 
makolo Awiri ndi achibale. Ndipo 
amene Mudagwirizana nawo 
Chipangano, apatseni gawo lawo. 
Ndithudi, Mulungu ndimboni Pa 
chilichonse. 2 

34. Amuna ndi ayang'aniri pa 
akazi Chifukwa choti Mulungu 
watukula Ena paulemerero 
pamwamba Pa ena chifukwa cha 
chuma chawo chimene apereka. 
Choncho, akazi Abwino ndi omwe 
ali omvera, Odzisunga ngakhale 
amuna Awo palibe pakuti 
Mulungu wawalamula 
Kudzisunga. Ndipo akazi omwe 
mukuopa Mnyozo wawo, 
achenjezeni; ndipo Kenako 









1 Apa akuletsa anthu kuchitirana dumbo. Koma chofunika nkuti munthu 
alimbike kugwira ntchito kuti nayenso apeze chomwe mnzake wapeza. Osati 
kumchitira dumbo ndi kumuda, pakuti iye palibe chimene wakulanda. 
Adagwira ntchito molimbika ndipo Mulungu wampatsa. Iwenso limbikira 
kugwira ntchito Mulungu akupatsa. Wopemphedwa ndi kupatsa ndiyemweyo 
Mulungu wathu. 

2 Kale Chisilamu chisadadze, munthu ankati akatenga mwana wamunthu wina 
nkumulera ankamuyesa mwana wake weniweni pomulowera chokolo 
pachilichonse ngati mwanayo atafa. Ngakhale makolo ake enieni ndi abale 
ake atakhalapo sadali kuwagawira chilichonse. Tsono Chisilamu chidathetsa 
mchitidwe umenewu ponena kuti munthu aliyense azimlowa chokolo ndi abale 
ake. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



178 



*jjfc-l 



i tL— ul ^jj-* 1 



achokereni pamphasa. (Apo ayi), 
akwapuleni; (kukwapula 
Kosavulaza) koma ngati 
Akukumverani, musawafunire 
njira yowavutitsira. Ndithu 
Mulungu ndi Yemwe ali 
wapamwamba, Wamkulu (kuposa 
inunonse). 1 

35. Ndipo (inu aweruzi) ngati 
muopa mkangano pakati pawo 
(pamwamuna Ndi mkazi wake), 
tumizani nkhoswe yakuchimuna 
ndi nkhoswe yakuchikazi. Ngati 
iwo atafuna kuyanjanitsa, Mulungu 
awapatsa mphamvu zoyanjanitsira 
Pakati pawo (okanganawo). 
Mulungu Ngodziwa nkhani 
zobisika, ndiponso Ngodziwa 
nkhani zoonekera. 






1 Apa akuti amuna ndi amene akhale ndi ulamuliro paakazi awo, 
powatsogolera kumiyambo yabwino. Osati kuti mkazi adzitukumule 
kwamwamuna wake poti iye ngophunzira zedi kapena wanzeru zochuluka 
kotero kuti mwamuna m'nyumba osamuyesa kanthu. Ngati atero ndiye kuti 
sakhala Asilamu owona. 

M'ndimemu atchulamonso makhalidwe ofunika kuti akazi akhale nawo. Ndipo 
atchulamo malangizo olangira nawo mkazi ngati samvera. Choyamba 
amchenjeze ndi mawu. Ngati kuchenjezako sikunathandize, asagone naye 
limodzi pamphasa. Ndipo ngati akupitirizabe kuchita mnyozo akupatsidwa 
chilolezo mwamuna kuti amlange pommenya mwakumuopyeza, osati 
kumenya komgulula nako mano. Komabe mahadisi amtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) akunena kuti asanaganize zommenya Ayeseyese 
kumkonza ponena naye mofewa ndi kumuonetsa kulakwa kwake. Ngati 
atalephera zonsezi, aitane anthu kuti adzawayanjanitse m'njira yabwino. 
Naonso anthuwo akhale ndi cholinga choyanjanitsa osati kupasula. 
Amunanso akuwachenjeza apa kuti iwo ndi amene ali ndi nyonga ndi udindo. 
Mulungu ndiye Wamkulu kuposa iwo amunawo. Mawu oti "Hafizatu Lilighaibi" 
maulama ena akulitanthauzira kuti "Akhale osunga chinsinsi," chimene chili 
pakati pa iwo ndi amuna awo ndi zonse zomwe zimachitika m'nyumba, pakuti 
nthawi zambiri akazi sakhalira kuulula zam'nyumba. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



179 



*j*-l 



t tL^Jl ^JJ— ' 



36. Ndipo mpembedzeni 
Mulungu, ndipo Musamphatikize 
ndi chilichonse; ndipo Achitireni 
zabwino makolo awiri, ndi 
Achibale, ndi ana amasiye ndi 
masikini Ndi mnansi woyandikana 
naye Nyumba, ndi wapadera 
wogundizana Naye nyumba, ndi 
mnzako wokhala Naye limodzi, 
ndi wapaulendo yemwe Alibe 
choyendera, ndi omwe manja anu 
akumanja apeza (adzakazi). 
Ndithudi, Mulungu sakonda 
wodzitukumula Ndi wodzitama. 1 

37. Omwe amachita umbombo 
ndi Kulamula anthu kuchita 
Umbombo ndi kubisa zabwino 
Zomwe Mulungu wawapatsa. 
Komatu osakhulupirira 
Tawakonzera chilango 
choyalutsa. 2 

38. Ndi omwe akupereka chuma 
Chawo modzionetsera kwa Anthu 
ndipo sakhulupirira Mulungu ndi 
tsiku lomaliza. Ndiponso yemwe 












M'ndime iyi akuwalamula anthu kuti apembedze Mulungu yekha ndi 
kumpempha lye yekha. Asapembedzenso china chilichonse, chamoyo 
kapena chakufa. Ndikuti awachitire zabwino makolo ake ndi onse amene 
awatchula m'ndimeyi. Sibwino kuthandiza anthu akumbali pomwe anthu 
omwe uli nawo pafupi sunawathandizepo. 

2 Kubisa zonse zomwe Mulungu wawapatsa kuli monga munthu kukhala ndi 
maphunziro koma osaphunzitsa anthu kotero kuti nkufa nawo popanda 
kuphunzitsapo aliyense. Kutero sibwino. Koma akafuna kukalowa m'munda 
wa Mtendere wa Mulungu nkofunika kuti achite zinthu zabwino ncholinga 
chokondweretsa Mulungu. Osati kuti anthu amuone ndi kumtama. Amene 
akuchita chinthu chabwino ncholinga choti anthu amtamande, sakalandira 
mphoto iliyonse pa tsiku lomaliza. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



180 



o *£\ 



t tL-jJl ^JJ— ' 



satana Angakhale bwenzi lake, 
ndithudi Ali ndi Bwenzi loipa. 

39. Kodi pakadakhala vuto lanji 
kwa Iwo ngati akadakhulupirira 
Mulungu ndi tsiku lomaliza 
Napereka zina mwa zomwe 
Mulungu wawapatsa? Ndipo 
Mulungu ali Wodziwa bwino za 
iwo. 

40. Ndithudi, Mulungu sachitira 
(anthu) zosalungama Ngakhale 
chinthu cholemera ngati Nyerere 
yaing'ono; ngati chinthucho chili 
Chabwino amachichulukitsa ndi 
kupereka Malipiro akulu 
kuchokera kwa lye. 

41. Nanga zidzakhala bwanji 
tikadzabweretsa Mboni pa 
mbadwo uliwonse 
ndikukubweretsa Iwe (Mneneri 
Muhammad {SAW}) kuti ukhale 
Mboni pa mbadwo uwu. 

42. Tsiku limenelo aja omwe 
sadakhulupirire Namunyoza 
Mtumiki, adzakhumba kuti Nthaka 
ikadafafanizidwa paiwo 
(Akwiriridwe, asaukitsidwe). 
Ndipo sadzatha kum'bisa Mulungu 
Nkhani iliyonse (m' zomwe 
Adachita m'moyo wapadziko). 

43. E inu amene 
mwakhulupirira! Musayandikire 
Swala uku muli oledzera, Mpaka 
mudziwe chimene mukunena; 






d&fc 















Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



181 



tjir) 



t «.l~*Jt *JJ~* 






Ngakhalenso pamene muli Ndi 
janaba (musapemphere Kufikira 
mutasamba) kupatula Amene ali 
paulendo(achite tayammam) Ngati 
muli odwala, kapena muli 
paulendo, Kapena m'modzi wanu 
wadza kuchokera Kuchimbudzi, 
kapena mwakhudza Akazi (m'njira 
yaukwati) ndipo Simunapeze 
madzi (osamba) chitani 
Tayammamu ndi dothi labwino; 
Lipakeni kunkhope kwanu ndi 
M'mikono mwanu. Ndithudi, 
Mulungu ngofafaniza machimo 
Anu, ndiwokhululuka. 

44. Kodi sukuwaona omwe 
adapatsidwa Gawo la (nzeru 
zozindikira) Buku (la Mulungu, 
omwe ndi Ayuda ndi Akhrisitu). 
Akuzisankhira kusokera ndiponso 
akufuna mutasokera (Kusiya njira 
yabwino) 1 



1 (Ndime 44-6) Apa akutchula kuipa kwina kwa Ayuda ndi Akhrisitu. Ayuda ndi 
Akhirisitu adali kusintha mawu omwe adalimo m'mabuku a Taurati ndi Injili, 
makamaka mawu amene adali kusonyeza za uneneri wa Muhammad 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye). Kapena adali kuwatanthauzira m'njira 
zina zolingana ndi zolinga zawo. Pamene adali kudza kwa Mtumiki 
Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) makamaka Ayuda, 
akawalalikira mawu achipembedzo, ankati; "Tamva, titsatira," pomwe 
m'mitima mwawo akuti "Sititsatira zonse zomwe ukunena. Koma 
tikungokunyenga chabe." Amati akadza nkumva momwe maswahaba adali 
kunenara ndi Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye), Mtumiki 
akawalalikira, amati "Ismaa ghayra musmaa" monga mwa chizolowezi cha 
Arabu akauzidwa mawu ofunika. Tanthuzo lake nkuti, "Imva siumvanso 
choipa kuchokera kwa ife ngati Mulungu afuna." Naonso Ayuda adali 
kumnenera Mtumiki mawu omwewa. Koma m'mitima mwawo akulinga 
tanthauzo lina. M'mitima mwawo amalinga kuti, "Siumva zabwino kuchokera 
kwa ife ngati Mulungu afuna. Koma zokusowetsa mtendere zokhazokha." 
Ndipo amati akabweranso Ayudawo nkumva maswahaba akumuuza Mtumiki 






Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



182 



o *jJH 



i $.L*Jl tjf* 



45. Ndipo Mulungu akudziwa 
Bwinobwino za adani Anu. Ndipo 
Mulungu Akukwanira kukhala 
Mtetezi. Mulungu akukwananso 
kukhala mthandizi. 

46. Mwa Ayuda alipo omwe 
amasintha mawu kuwachotsa 
m'malo mwake. Ndipo amanena 
(Chabe ndi milomo yawo); 
"Tamva;" (pom we Mitimayawo 
ikunena) : "Tanyoza". (ndipo 
Akunena kuuza Mtumiki): "Imvera 
koma wosamveredwa (ndipo 
pakati pakuyankhula Kwawo 
amanena mawu akuti) 'Raaina' 
(Ncholinga chomnenera kuti iye 
ndimbutuma). Ndipo mokhotetsa 
zoyankhula zawo (kuti Akhale 
ngati akumunenera zabwino 
pomwe Akumtemberera) ndi 
cholinga chotukwana 
Chipembedzo (cha Chisilamu). 
Akadakhala kuti Iwo adanena; 
"Tamva ndipo tarn vera; ndipo 
Imva, utiyang'anire" (mmalo 
monena kwawo Kwakuti 
'Raaina'), zikadakhala zabwino 
ndizolingana kwa iwo. Koma 
Mulungu adawatemberera 






kuti; "Raaina". Kutanthauza kuti, "Tiyang'ane anthu ako ndidiso lachifundo," 
iwonso amayankhula mawu omwewa, koma mokhotetsa pang'ono mpaka 
kusinthika tanthauzo lake. M'chiyankhulo cha chiyuda limatanthauza kuti "E 
iwe mbutuma!" Ndipo iwo m'kunena kwawo amalinga tanthauzo limeneli. 
Choncho Asilamu anawauza kuti azigwiritsira ntchito mawu oti "Unzuruna." 
Ndipo mawuwa tanthauzo lake ndilofanana. Koma mawu awa sakadatha 
kuwakhotetsa. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



183 



o ljk\ 



t «.L«Jl djj~*> 



chifukwa cha kusakhulupirira 
kwawo. Sakhulupirira koma 
pang'ono basi. 

47. E inu amene mwapatsidwa 
Buku! Zikhulupirireni zomwe 
tavumbulutsa Zikutsimikizira 
zomwe muli nazo Tisanazisinthe 
nkhope zanu ndi Kuzitembenuzira 
kumbuyo kwake, Kapena 
tisanawatemberere monga momwe 
tidawatemberera omwe 
Sadalemekeze kupatulika kwa 
tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la 
Mulungu ndilochitikadi. 

48. Ndithudi Mulungu 
sangakukhululuke Kuphatikizidwa, 
koma amakhululuka (Machimo 
ena) osati amenewa kwa Amene 
wamfuna. Ndipo amene 
Angamphatikize Mulungu, 
Ndithudi, wadzipekera uchimo 
waukulu. 

49. Kodi sukuwaona omwe 
akudziyeretsa okha? Koma 
Mulungu amamyeretsa amene 
wamfuna Pomulimbikitsa kuchita 
zabwino. Ndipo 
sadzaponderezedwa angakhale 
Ndikachinthu kochepa konga 
kaulusi kokhala mkati mwakhokho 
latende. 1 






9.1" . '\'ll "['•*'&')> it\ 






1 Ayuda adali kunyada chifukwa choti iwo adali nawo Aneneri, ndiponso 
makolo awo omwe adali olungama. Ankati: "Poti makolo athu adali olungama 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



184 • *>• 



t f-L^Jl *JJ** 



50. Taona, momwe akumpekera 
Mulungu bodza! Ndipo izi 
zikukwana kukhala tchimo 
loonekera! 

51. Kodi sukuwaona omwe 
apatsidwa Gawo la nzeru 
zozindikira Buku (La Mulungu)? 
Amakhulupirira Mafano ndi 
asatana, ndipo akumati kwa amene 
sadakhulupirire "Awa ali panjira 
yoongoka kwabasi kuposa 
okhulupirira (Asilamu)" 1 

52. Iwo ndi omwe Mulungu 
Wawatemberera. Ndipo amene 






palibe chochititsa mantha paife. Utchimo uliwonse umene ife tingachite 
Mulungu adzatikhululukira ngakhale utchimowo utakhala waukulu chotani." 
Iwo ankadzitchanso kuti adali okondedwa a Mulungu. Ndipo iwowo ngomwe 
akuwatchula m'ndime iyi kuti "Kodi saona amene akudziyeretsa okha ndi 
mawu okha ochokera m'milomo popanda kuchita zimene adawalamula ndi 
kusiya zomwe adawaletsa?" 

Mwa Asilamu aliponso ena omwe ali ndi maganizo onga amenewa. 
Amangonyadira zochita zamakolo awo popanda kutsanzira chikhalidwe 
chamakolo awowo. 

1 Mawu oti "Jibti ndi Twaghut" amanena za chinthu chomwe anthu 
akuchipembedza chamoyo kapena chakufa chomwe sichili Mulungu weniweni 
monga momwe lilili dzina loti Shetani. Iloli limatchulidwa kwa aliyense amene 
akusokeretsa anthu ku njira ya Mulungu. Chifukwa cha kuipidwa ndi Asilamu, 
Ayuda adapita ku Makka kukapalana ubwenzi ndi Akuraishi ndi Arabu ena 
opembedza mafano kuti athandizane nawo kumthira nkhondo Mtumiki 
Muhammad(SAW) pamodzi ndi omtsatira ake kuti achithetseretu chipembedzo 
cha Chisilamu. Choncho akuluakulu a Chiyuda atafika ku Makka adagwadira 
mafano ncholinga chofuna kukondweretsa Akuraishi pomwe Ayudawo adali 
eni mabuku omwe salola kupembedza mafano. Adawalimbikitsanso Akuraishi 
aja powauza kuti: "Zochita zanu pachipembedzo chanu nzabwino kuposa 
zochita za Muhammad pachipembedzo chake chimene wadza nacho." Iwo 
amanena izi akudziwa kuti akunama. Cholinga chawo kudali kupeza 
chithandizo kwa iwo kuti athetse Chisilamu chifukwa chakudzazidwa ndi njiru 
m'mitima mwawo ponena kuti: "Nchotani kuti Muhammad (SAW) alandire 
chisomo chauneneri?" Iwo ankachita izi ngati kuti ufumu wa Mulungu udali 
m'manja mwawo kuti iwo ndi amene amagawa zachifundo cha Mulungu, 
chonsecho, Mulungu amapereka kwa yemwe wamfuna. lye amachita chimene 
wafuna. Safunsidwa ndi aliyense pachimene wachita. Koma iwo amafunsidwa. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



185 



frjJrl 



i *L*Jt 3jj-«* 



Mulungu wamtemberera, 
Simungathe kumpezera 
wompulumutsa. 

53. Kodi ali ndi gawo la ufumu 
(Wa Mulungu? Nchifukwa Ninji 
akunyasidwa munthu wina 
akaninkhidwa utumiki)? 
Zikadatero ndiye kuti 
sakadawapatsa anthu ngakhale 
kochepa kwambiri monga Khokho 
latende. 1 

54. Kodi akuchitira anthu 
dumbo Pazomwe Mulungu 
wawapatsa ndiufulu wake? 
Choncho tidalipatsa banja la 
Ibrahim Buku ndi nzeru. Ndipo 
tidawapatsa ufumu waukulu. 

55. Choncho alipo ena mwaiwo 
amene anazikhulupirira izi, 
ndiponso alipo ena mwaiwo omwe 
adziika nazo kutali. Ndipo 
Jahanama ikukwanira kukhala 
moto waukali wowatentha. 

56. Ndithu, amene 
sadakhulupirire zizindikiro zathu, 
tidzawalowetsa kumoto. Nthawi 






±9*' K*' 94999 s s'\ 9*&99*< 






1 (Ndime 53-4) Ndime izi zikusonyeza kuti zonse zimene Ayuda ankawachitira 
Asilamu nchifukwa chadumbo basi. Ankawawidwa nawo mitima chifukwa 
choti Asilamu apeza chisomo cha Mulungu. Palibe chinthu chimene 
chimaletsa anthu kutsata choonadi kuposa dumbo. Ngati utamchitira dumbo 
munthu sungalole kutsata langizo lake lililonse ngakhale litakhala lopindulitsa 
pano padziko lapansi ndi tsiku lomaliza Dumbo ndi lomwe likuletsa anthu 
ambiri kutsata choonadi. Choncho tiyeni tipewe khalidwe limeneli kuti titsatire 
choonadi paliponse pamene chachokera. Ndikutinso tipeze mtendere 
m'mitima mwathu. Dziwani kuti dumbo nlomwe lidamchititsa Iblis kukhala 
wotembereredwa. 



Siirat4. An-Nisa' Juzu 5 



186 • *>» 



t tL— Jl <*JJ-" 









WU 



esa® 



iliyonse yomwe makungu awo 
adzikapserera tidzidzawasinthira 
makungu ena kuti adzapitirize 
kulawa chilango. Ndithudi, 
Mulungu Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 1 

57. Ndipo amene akhulupirira 
ndikuchita zabwino, 
Tidzawalowetsa m'minda mom we 
mitsinje ikuyenda pansi ndi 
patsogolo pake. Adzakhala 
mmenemo muyaya. Ndipo Iwo 
adzapeza mmenemo akazi 
oyeretsedwa (ku Uve wamtundu 
uliwonse) ndi kuwalowetsa ku 
Mithunzi yabwino kwambiri. 

58. Ndithudi, Mulungu 
akukulamulani Kubweza kwa eni 
zomwe mwakhulupirika nazo. 
Ndipo pamene mukuweruza 
pakati paanthu, Weruzani 
mwachilungamo. Ndithu, 
malangizo amene Mulungu 
akukulangizani, ngabwino 
Kwambiri. Ndithudi, Mulungu 
Ngwakumva, Ngoona. 2 



1 (Ndime 56-7) Apa akutchula zamalipiro a anthu ochita zabwino ndi malipiro 
a anthu ochita zoipa umu ndi momwe ulili ulaliki wa Qur'an. Qur'an 
ikafotokoza za anthu ochita zoipa imatsatiza pompo kufotokoza zotsatira za 
anthu ochita zabwino. Pamenepa akunena kuti aliyense adzalandira 
malipiro a zochita zake, abwino kapena oipa. Sakawomboledwa chifukwa 
chaubwino wa munthu wina. Zochita zake ndizo zikamuombola kapena 
kukamponya kuchionongeko. 

2 Pali anthu ena amene amati anzawo akawasungitsa zinthu kuti akhulupirike 
pazimenezo, mwini zinthu uja akafa kapena kuti panalibe umboni wokwanira, 
amazitenga zinthuzo poganizira kuti palibe chomwe chingawavute popeza 
mwini zinthuzo adamwalira ndipo umboni wokwanira palibe. Chikhalidwe 
chotere si cha Chisilamu, Chisilamu sichifuna machitidwe otere. 






Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



187 



3 frjA-l 



i s.l*Ji ^j-* 



59. E inu amene 
mwakhulupirira! Mumvereni 
Mulungu ndiponso Mumvereni 
Mtumiki, ndi omwe ali ndi udindo 
painu. Ngati Mutatsutsana 
pachinthu chilichonse, Chibwezeni 
kwa Mulungu ndi Mtumiki Wake, 
Ngatidi mukukhulupirira Mulungu 
ndi tsiku lomaliza, kutero 
ndibwino; Ndipo zotere zili ndi 
zotsatira zabwino. 1 

60. Kodi sukuwaona omwe 
akungonena chabe kuti 
akhulupirira zomwe 
zavumbulutsidwa kwa iwe ndi 
zomwe zidavumbulutsidwa 
patsogolo pako, Pomwe iwo 
akufuna kuti akaweruzidwe ndi 
maweruzo osagwirizana ndi 
Shariya, Pomwenso alamulidwa 
kukana njira Zotere? Koma satana 
akufuna Kuwasokeretsa, kusokera 
kwakutali. 

61. Ndipo akauzidwa: "Idzani 
Kuzomwe Mulungu 
wavumbulutsa, Ndipo (idzani) kwa 
Mtumiki." Uwaona achinyengo 
akudziika kutali kwabasi ndi iwe. 






oji^s %;, Iv* tattoo ujj 






£\*9 f 9 *ii* ' * 9*9' 



1 Aliyense amene amdzoza utsogoleri nkofunika kuti anthu amumvere ngati 
iye akulamula zabwino. Pagulu la anthu ngati sipakhala mtsogoleri 
womumvera, ndiye kuti pamapezeka zisokonezo ndi ziwawa kotero kuti zinthu 
zawo siziyenda bwino. Chisilamu sichiloleza machitidwe achipolowe ndi 
ziwawa. Chisilamu chimakonda bata ndi mtendere ndi kuti pasapezeke anthu 
ena owachenjerera anzawo. Komatu atsogoleriwo awamvere akalamula mwa 
chilungamo popanda kulakwira Mulungu. Koma ngati akulakwira Mulungu 
asawamvere. Pamenepo atsate chomwe Mulungu wawalamula ndi Mtumiki 
Wake. 



Siirat 4. An-Nisa' Juzu 5 



188 



o fjA-i 



t «.L*Jt 3jj~* 



62. Kodi zingakhale bwanji 
litawabwerera vuto chifukwa cha 
zomwe manja awo adatsogoza? 
Kenako nkukudzera (iwe Mtumiki) 
uku akulumbira: "Tikulumbira 
Mulungu; Sitinafune china 
chilichonse koma zabwino zokha 
ndi chimvano." 

63. Iwo ndi omwe Mulungu 
akudziwa zomwe zili mmitima 
mwawo. Choncho dzipatule kwa 
iwo, Ndipo alangize ndi kuwauza 
Mawu ogwira mtima. 

64. Ndipo sitidamtumize 
Mtumiki aliyense koma Kuti 
azimveredwa mwa lamulo la 
Mulungu. Ngati akadakudzera 
pamene adadzichitira okha Zoipa, 
(chifukwa chokafuna chiweruzo 
cha Satana) napempha 
chikhululuko kwa Mulungu (Naye) 
Mtumiki nkuwapemphera, 
ndithudi, Akadampeza Mulungu 
ali wolandira kulapa kwawo ali 
Wachisoni. 

65. Ndikulumbira (m'choonadi 
cha) Mbuye wako, Iwo 
sangakhale okhulupirira moona 
Pokhapokha akuyese muweruzi 
wawo Pazomwe akukangana 
pakati pawo. Kenako Asaone vuto 
mmitima yawo pazomwe 
waweruza, Ndipo adzipereke 















Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



189 • *>» 



t tL-jl djjMtl 



kwathunthu (pogonjera Chiweruzo 
chako). 1 

66. Ndipo ngati 
tikadawakakamiza kuti: "Dzipheni 
nokha," kapena: "Tulukani 
m'nyumba Zanu; (Mupite 
kunkhondo kapena musamuke)," 
Sakadachita zimenezo kupatula 
ochepa Mwa iwo. Koma 
akadachita zomwe auzidwa, 
zikadakhala zabwino kwa iwo. 
Ndipo zikadawalimbikitsa 
Kwambiri (Chisilamu chawo) 

67. Ndipo zikadatero, 
Tikadawapatsa malipiro Aakulu 
ochokera kwa Ife. 

68. Ndiponso tikadawatsogolera 
Ku njira yoongoka. (Yokawafikitsa 
ku Munda wamtendere). 

69. Ndipo amene angamvere 
Mulungu Ndi Mtumiki wake, 
iwo wo Ndi omwe adzakhale 
pamodzi ndi Omwe Mulungu 
adawadalitsa, Kuyambira aneneri, 
Olungama, maShahidi(asilamu 
ofela kunkhondo) ndi anthu 






®Q&J$&&&$$& 



i&SRJv&i&Z 



© 



** 9 



1 Ngati anthu atakangana pachinthu ena nati chimenechi nchofunika pomwe 
ena akuti nchosafunika, onsewo abwere nkuyang'ana kuti mawu a Mulungu 
ndi mawu a Mtumiki akunena chiyani pachinthu choterecho. Tsono akapeza 
malangizo a Mulungu ndi Mtumiki pachimenecho awatsatire. Aliyense waiwo 
asakhumudwe poona kuti zomwe amalimbikira sindizo zomwe Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) adaphunzitsa. Koma agonjere 
kwathunthu kuzophunzitsa za Mtumikizo. Chilichonse chimene Mtumiki 
walangiza asawiringule nacho. Koma angotsatira basi. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



190 ° *>■' 



t $-L— Jl 5jj-»» 



abwino. Taonani ubwino wokhala 
Nawo pamodzi iwowo! 1 

70. Umenewo ndiubwino 
wochokera Kwa Mulungu. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa mokwanira. 

71. "E inu amene 
mwakhulupirira! Khalani 
ochenjera (ndi adani anu; 
musanyengedwe Nawo). Pitani 
(kunkhondo) gulu limodzilimodzi, 
Kapena pitaniko nonsenu pamodzi 
(monga Momwe Mtumiki 
angakulangizireni) . 

72. Ndipo alipo ena mwainu 
otsalira M'mbuyo sapita 
kunkhondo, (Ndiponso amaletsa 
anzawo). Ngati Vuto litakupezani, 
(yense waiwo) amanena: 
"Mulungu wandichitira chisomo 
Posakhala m'gulu lawo 
kumeneko." 

73. Koma ubwino wa Mulungu 
ukakupezani (monga Kupeza 
chuma chambiri chosiidwa ndi 
adani, Kapena kupambana 
kumene) amanena ngati kuti 
Padalibe chikondi pakati panu ndi 
pakati Pake, "Kalanga ine! 












1 Aliyense wochita zabwino zomwe nzovomerezeka ndi malamulo a Chisilamu 
akalowa Kumunda Wamtendere. Ndipo aliyense amene akalowe kumundako, 
akakumana ndi anzake kumeneko. Ndipo nthawi zina azikakhala nawo 
pamodzi ngakhale kuti malo awo okhalamo adzakhala osiyanasiyana 
chifukwa chakulekana maulemerero awo amene adawapeza kupyolera 
m'zochita zawo. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



191 



o *jk-\ 



i *L«Jl *JJ- t ' 



Ndikadakhala nawo Pamodzi 
pankhondo imeneyi, (ndiye kuti) 
Ndikadapambana; kupambana 
kwakukulu." 

74. Choncho, amenyane panjira 
ya Mulungu omwe akugulitsa 
moyo (Wawo) wadziko lapansi ndi 
Tsiku lomaliza. Ndipo amene 
angamenyane panjira ya Mulungu, 
Kenako ndikuphedwa kapena 
Kupambana tidzampatsa malipiro 
aakulu. 

75. Mwatani inu osamenyana 
panjira ya Mulungu, 
(ndikuwapulumutsa) Omwe ali 
ofooka, aamuna ndi Aakazi ndi 
ana, omwe akunena: "Mbuye 
wathu! Titulutseni m'mudzi Uwu 
omwe anthu ake ndiopondereza; 
Ndipo tipatseni mtetezi wochokera 
Kwa Inu; ndiponso tipatseni 
Mthandizi wochokera kwa Inu." 1 

76. Amene akhulupirira, 
akumenya (nkhondo) Panjira ya 
Mulungu. Koma amene 
Sadakhulupirire, akumenya 






^Lii'da'-ft 






si 



®vj^'^y&&i\% 






Pamene Mtumjki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adasamuka ku 
Makka kukakhala ku Madina, Asilamu ena aamuna ndi aakazi adatsalira ku 
Makka chifukwa chakuti abale awo adawaletsa. Ndipo chifukwa chakufooka 
kwawo sadathe kuthawa mozemba namangokhala konko ku Makka 
akuwachitira zoipa zambiri ndi kumawanyoza. Choncho Asilamu adawauza 
kuti ngati kuzakhale kololezedwa kuchita nawo nkhondo Akuraishi a m'Makka 
adzamenyane nawo Akuraishiwo molimba kufikira adzawapulumutse. Asilamu 
adakwaniritsa lonjezolo. Adamenya nkhondo mpaka kugonjetsa mzinda wa 
Makka ndi kuwapulumutsa anzawo amene adali kupempha Mulungu kwa 
nthawi yaitali kuti awapulumutse ku anthu oipa. 



Surat 4. An-Nisa' 



Juzu 5 



192 



o ^\ 



t *L**J1 ^JJ— ' 



(nkhondo) Panjira ya Satana. 
Choncho menyanani Ndi abwenzi 
a Satana. Ndithudi, Ndale za 
Satana nzofooka. 

77. Kodi sukuwaona omwe 
Adauzidwa kuti: "Aletseni manja 
anu (kumenyana ndi 
osakhulupirira mpaka lidze lamulo 
lakumenyana)? Koma tsono 
pempherani Swala ndikupereka 
chopereka basi. Koma pamene 
adakakamizidwa Kumenyana, 
pompo gulu Una la Iwo lidaopa 
anthu (Osakhulupirira) Ngati 
likuopa Mulungu kapena 
kuposerapo. Ndipo adati: "Mbuye 
Wathu! chifukwaninji 
mwatikakamiza kumenyana? Ha! 
Mukadatichedwetsa Kufikira * 
nyengo yochepa, (Zikadakhala 
Bwino)." Nena: "Chisangalalo 
cham'dziko n'chochepa. Koma 
tsiku Lomaliza ndilabwino 
kwambiri kwa Amene akuopa 
(Mulungu). Ndipo 
Simudzaponderezedwa ngakhale 
pachinthu Chaching'ono monga 
ulusi Wakhokho la tende!" 

78. Paliponse pamene 
mungakhale Imfa ikupezani 
ngakhale mutakhala M'malinga 
olimba ngati ubwino Utawafika 
(Amushirikina ndi Amunafikina) 
amati: "Ubwinowu, Ukuchokera 
kwa Mulungu." Koma choipa 



©S^^yl^lu^f)) 









Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



193 



o *jA-i 



£ 5-L-Jl 5jj-** 



chikawafikira, Amati: "Ichi 
chachitika chifukwa chaiwe 
(Muhammad)." Nena: "Zonse 
zachokera Kwa Mulungu." Kodi 
ngotani anthu Awa, sangathe 
kuzindikira nkhani? 1 

79. Chabwino chimene 
chakufikira (iwe munthu) Ndiye 
kuti chachokera kwa Mulungu. 
Koma Choipa chimene chakufikira 
ndiye kuti Chachokera kwa iwe 
mwini (chifukwa cha Zochita zako 
zoipa). Ndipo takutumiza (iwe 
Muhammad) kwa anthu kukhala 
Mtumiki. Ndipo Mulungu 
ndimboni yokwana. 

80. Yemwe angamvere 
Mtumiki ndiye kuti wamvera 
Mulungu, (chifukwa chakuti zonse 
zomwe iye Akulamula 
nzotumidwa ndi Mulungu). Ndipo 
Amene atembenukire kutali 
(kunyoza iwe, Ndiye kuti zoipa zili 
paiye mwini). Sitidakutumize 
iweyo kukhala kapitawo pa iwo. 

81. Amati: "Tikumvera." Koma 
akachoka Kwaiwe, gulu lina la iwo 
limapangana Usiku zosagwirizana 
ndi zomwe Ukunena (pamaso 
pawo). Koma Mulungu akulemba 
zonse Zomwe akupangana. 
Choncho Apatukire ndipo 















1 Ndime iyi ikutsimikizira kuti imfa njosathawika. Paliponse pamene munthu ali 
impeza. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



194 • *j*-i 



£ £L*Jl OjJ~*> 



yadzamira kwa Mulungu. Ndipo 
Mulungu Ndimtetezi wokwanira. 

82. Kodi bwanji sakuiganizira 
Qur'an? Ndipo ikadakhala kuti 
siikuchokera Kwa Mulungu, 
ndithudi, mmenemo Akadapeza 
kusiyana kwambiri, 
(Mukadapezeka mawu otsutsana; 
Koma Qur'an siili choncho). 1 

83. Ndipo chikawadzera 
chinthu Chilichonse chachitetezo 
kapena Mantha, amachifalitsa. 
Ngati Akadachibweza kwa 
Mtumiki Ndi kwa omwe all ndi 
udindo Pa iwo, akadachidziwa 
omwe Amafufuzafufuza zinthu 
mwa Iwo (kuti kodi nzoyenera 
Kuzifalitsa kapena ayi). 









1 M'ndime iyi akuti Qur.an iyi mawu ake ngolingana. Siotsutsana ayi. Ndipo 
palibe amene angabweretse mtsutso wakuti mawu ena omwe ali m'bukuli 
ngabodza pachifukwa chakutichakuti. Palibe buku lomwe munthu adalemba 
lomwe lidabweretsa mtsutso weniweni wakuti Qur'an simawu a Mulungu 
pachifukwa chakutichakuti. Ndipo silidzapezeka buku lotero mpaka dziko 
lapansi lidzatha. Koma mwina anthu akhoza kumayankhula chabe popanda 
kubwera ndi mtsutso weniweni wokhala ndi umboni wooneka. Kuona kwa 
Qur'an kwatsimikizika pazinthu izi:- Qur'an idafotokoza nkhani zakale zomwe 
zidachitika Mtumiki Muhammad (SAW) asanabadwe pomwe iye sankadziwa 
kulemba ndi kuwerenga mabuku. Quran idafotokozanso zamtsogolo. Ndipo 
zina mwaizo zaonekera kale poyera: (1) Qur'an idati: "Chinthu chilichonse pali 
chachimuna ndi chachikazi". Yang'anani ndime ya 36 ya Surat Yasin. (2) 
Kuti dziko lapansili lidalumikizana ndi kumwamba monga ikufotokozera Surat 
Anbiyaa ndime ya 30. (3) Kuti moyo umadalira madzi, monga momwe ndime 
ya 30 ya m'Surat Anbiyaa ikulongosolera. (4) Kuti anthu amene ali kutali 
kwambiri adzatha kumva zimene anthu ena akutali akunena. Monga momwe 
ndime ya 44 ya m'Surat Aaraf. (5) Ndi kuti anthu adzakwera kumwamba 
monga momwe ikulongosolera ndime ya 13 yam'Surat Jathiya. m'Qur'an 
muli zambiri zimene adafotokoza kuti zidzachitika mtsogolo. Ndipo zambiri 
mwa izo zachitikadi, anthu aziona. Ndipo zonsezi zikutsimikizira kuti Qur'an 
ndi mawu a Mulungu. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



195 



O *>! 



i *L«Ji Sjj-*' 



Pakadapanda ubwino wa Mulungu 
ndi chifundo chake Pa inu, 
ndithudi, mukadamtsatira Satana 
kupatula ochepa. 

84. Choncho menya nkhondo 
panjira Ya Mulungu, 
suukukakamizidwa (Za anthu ena) 
koma iwe mwini, Ndipo 
akhwirizire Asilamu. Ndithu 
Mulungu angatsekereze mtopola 
Wa omwe sadakhulupirire. Ndipo 
Mulungu Ngwaukali Kwambiri 
Pomenya nkhondo ndiponso 
Wolanga kwabasi. 

85. Amene angampemphere 
(Mnzake) pempho labwino 
(Lothandizira pazabwino) 
adzapeza Gawo mmenemo. Ndipo 
amene Angampempherere 
pemphero Loipa, adzapeza gawo 
m'zoipazo. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 1 

86. Ndipo pamene 
mwalonjeredwa; Kulonjeredwa 
kwamtundu uliwonse (Salam) 
Vomerani ndi malonje abwino 
oposa Amenewo, kapena Bwezani 
ofanana Nawo. Ndithudi, Mulungu 
Ngowerengera chinthu 
chilichonse. 






<g> 



»ffi« 



O&iJ 









M'ndime iyi akuwalangiza anthu kuti azithandizana pazabwino zokha. 
Azithandizana pazochita ndi zonena. Munthu akokere anzake kuzinthu 
zabwino mmene angathere. lyenso mwini athandize ena pazinthu zabwino. 
Akachita izi adzalandira mphoto yaikulu kwa Mulungu. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



196 



o *jfcl 



t tl~jS\ $jj-»» 



87. Mulungu! Palibe 
wopembedzedwa Mwachoonadi 
koma lye basi. Ndithudi, 
Adzakusonkhanitsani tsiku 
lachiweruzo Lopanda chikaiko 
mwailo. Kodi ndi Mawu a ndani 
angakhale oona Kuposa a 
Mulungu? 

88. Kodi mwatani inu pokhala 
magulu awiri Pankhani ya 
Amunafikina (achinyengo) Pomwe 
Mulungu wawatembenuza 
chifukwa (Cha zoipa) zomwe 
achita? Kodi mukufuna Kuti 
mumuongole amene Mulungu 
wamlekerera Kusokera? Ndipo 
amene Mulungu Wamsokeretsa, 
simungathe kumpezera njira 
(yomuikira kuchilungamo). 

89. (Osakhulupirira a Chiarabu) 
akufuna Kuti mukadakhala 
osakhulupirira Monga momwe iwo 
sadakhulupirire Tero kuti mukhale 
ofanana. Musawachite kukhala 
abwenzi Mpaka asamuke chifukwa 
cha Chipembedzo cha Mulungu. 
Koma Ngati anyoza, agwireni ndi 
kuwapha Paliponse mwawapeza 
(monga Momwe akukuchitirani 
inu). Ndipo musamuyese mtetezi 
Ngakhale mthandizi aliyense wa 
iwo. 

90. Kupatula omwe 
akugwirizana Ndi anthu amene 
pali pangano Pakati panu ndi iwo, 












, J&&S\v)*&.{Jl$ % 



Surat 4. An-Nisa' 



Juzu 5 



197 • *>» 



i $.L-Ji *jj^ 



kapena Omwe akudza kwainu uku 
zifuwa Zawo zili zobanika 
kumenyana Nanu, kapena 
kumenyana ndi Anthu awo. 
(Oterewo musamenyane nawo). 
Ngati Mulungu akadafuna, 
Akadawakhwirizira painu, 
choncho Akadamenyana nanu. 
Ngati Atakupewani, osamenyana 
nanu ndipo Nkukupatsani 
mtendere, ndiye kuti Mulungu 
Sadakupangireni njira paiwo 
(yakuti Mumenyane nawo). 

91. Muwapeza ena omwe 
akufuna kupeza Mtendere kwa inu 
ndi kupeza mtendere Kwa anthu 
awo. Nthawi iliyonse 
Akabwezedwa ku ukafiri (Ndi 
anzawo osakhulupirira), 
Amagweramo mwamtheradi 
(nkuyamba Kumenyananso ndi 
inu) ngati sadzipatula Kwa inu 
ndipo osakupatsani Mtendere ndi 
kutsekereza manja awo, Agwireni 
ndi kuwapha paliponse pamene 
Mwawapeza (monga momwe iwo 
Akuchitira kwa inu) ndipo 
Takupangirani chisonyezo 
Choonekera pa iwo 

92. Ndipo sikoyenera kwa 
Msilamu kupha Msilamu (Mnzake 
mwadala) pokhapokha mwangozi. 
Ndipo yemwe wapha Msilamu 
mwangozi, apereke Ufulu kwa 



9' X*5VTV >\ £.t*»Ul »*<»'• 



„9S 9t9 9j$. I 9 S 9?9\9&l' *? 99 % 9 <> 






Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



198 « *>■ 



£ *L*Jl djj—» 



kapolo wa Chisilamu ndi dipo 
lomwe Alipereke kwa ofedwawo 
pokhapokha akakana Okha 
(amulowa mmalo a womwalilayo), 
monga M'njira ya sadaka. Ngati 
wophedwayo ndi Mnansi wa adani 
anu pomwe ali Msilamu, Perekani 
ufulu kwa kapolo wa Chisilamu, 
(palibenso dipo lina). Ngati 
wophedwayo ndi mmodzi Wa 
anthu omwe pakati panu ndi Iwo 
pali chipangano (chosamenyana 
Nkhondo), ndiye kuti 
amulowammalo Ake apatsidwe 
dipo; Apatsidwenso ufulu kapolo 
wa Chisilamu. Ndipo ngati 
sadapeze (zoterozo), Asale miyezi 
iwiri yotsatana. Iyo ndiyo Njira 
yolapira (pautchimo Wotere) 
yochokera kwa Mulungu. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa Ngwanzeru 
zakuya. 

93. Ndipo amene angaphe 
Msilamu mwadala, Mphoto yake 
ndi Jahanama; Mmenemo 
adzakhala Muyaya. Ndipo 
Mulungu amkwiira Ndi 
kumtemberera ndi kumkonzera 
Chilango chachikulu. 

94. "E inu amene 
mwakhulupirira! Mukayenda 
Panjira ya Mulungu, musachite 
chinthu Pokhapokha mutaonetsetsa 
bwino. Ndipo Musanene kwa 
amene akukulonjerani Salamu 









Q®S&£ 



"*\£ 



U^jUuJI *j£\&f Uj^W> 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



199 



O *>! 



t ^L^Jl Ojj-*' 



(kuti): "Sindiwe Msilamu," 
(Nkumupha). Mukufuna zinthu 
Zamdziko lapansi komatu Kwa 
Mulungu kuli zopeza zambiri. 
Umo ndi momwe inunso mudalili 
Kale; koma Mulungu 
adakuchitirani Chifundo (choncho 
mudalowa m'Chisilamu. 
Penyetsetsani bwinobwino). 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa 
bwinobwino Nkhani zonse zimene 
muchita. 

95. Sangafanane Asilamu omwe 
Akukhala osapita kunkhondo 
Pomwe sali ovutika, ndi amene 
Akumenya nkhondo yoyera 
Panjira ya Mulungu ndi Chuma 
chawo ndi miyoyo yawo. Mulungu 
wawatukula paubwino Ndi 
paulemerero amene akuchita Jihadi 
ndi chuma chawo ndi Miyoyo 
yawo kuposa okhala. Koma 
onsewo Mulungu wawalonjeza 
Zabwino. Koma wawapambanitsa 
Ochita Jihadi malipiro Aakulu 
Kuposa ongokhala. 

96. Adzapata ulemerero 
waukulu ochokera Kwa iye ndi 
chikhululuko ndi chisoni. Ndipo 
Mulungu Ngokhululuka kwambiri, 
Ngwachisoni zedi. 

97. Ndithudi amene angelo 
atenga miyoyo yawo, Ali 
odzichitira okha zoipa 















Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



200 



o *jA-i 



t s-L-uil ^J-*' 



(posasamuka ku 
Makka),adzawauza kuti: 
"Mudachitanji (Pachipembedzo 
chanu?)" Iwo adzati: "Tidali 
Ofooka ndi oponderezedwa 
padziko: (Choncho Sitidathe 
kuchita mapemphero Athu)." 
(Angelo) adzati: "Kodi Dziko la 
Mulungu silidali lotambasuka 
kotero Kuti inu nkusamukira 
kwinam'menemo?" Iwowo malo 
awo ndi Jahanama. Taonani Kuipa 
kwa malo obwelera. l 

98. Kupatula omwe adali 
ofooka Kwenikweni amuna Ndi 
ana omwe sangathe kuchita Ndale 
yamtundu uliwonse, ndipo 
Sangathe kulondola njira (Yonkera 
ku Madina). 

99. Choncho iwo ndithudi 
Mulungu Angawafafanizire, Pakuti 
Mulungu ngofafaniza Machimo, 
wokhululuka. 

100. Ndipo amene angasamuke 
panjira ya Mulungu (Chifukwa cha 



®}jK*a* oA*o >^A>- 



^ )f\ * ' '* 9' *' &'»**>? 9 






(Ndime 97-9) Kalelo Mtumiki (SAW) atasamukira ku Madina pamodzi ndi 
omtsatira ake Asilamu adawalamula kuti asamukire ku Madinako kusiya 
nyumba zawo, chuma chawo, abale awo ndi ana awo. Izi zidali chonchi 
chifukwa iwo akanakhalabe m'midzi yawo Pansi pautsogoleri wa anthu 
osakhulupirira sakanatha kukwaniritsa malamulo a Chisilamu. Tero Chisilamu 
chake sichikanakhala ndi ntchito. Ndipo Chisilamu chopanda ntchito si 
Chisilamunso. Tero nchifukwa chake apa akuwadzudzula amene 
sanasamuke kuti adzafa ndi imfa yoipa kupatula okhawo amene sanapeze 
njira yosamukira ku Madina chifukwa chakufooka kwa matupi awo.Amenewa 
madandaulo awo akhoza kuwavomera. Koma chachikulu nkuti ayesetse 
kusamukira ku Madina. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



201 • *>» 



i s-L-Jl *jj** 



chipembedzo chake,) apeza malo 
Ambiri m'dzikomo othawira 
ndikupeza bwino. Ndipo amene 
angatuluke m'nyumba mwake kuti 
Asamuke chifukwa cha Mulungu 
ndi Mtumiki Wake, kenako 
nkumpeza imfa (m'njira), ndithu, 
Malipiro ake atsimikizika kwa 
Mulungu. Ndithudi, Mulungu 
ngokhululuka kwambiri, 
Ngwachisoni chambiri. 1 

101. Ndipo ngati mukuyenda 
padziko, Sikulakwa kwainu 
kufupikitsa Swala ngati mukuopa 
kuti Angakusokonezeni omwe 
Sadakhulupirire. Ndithudi, 
Osakhulupirira ndi adani Anu 
oonekera. 



f 






9 9 '\l9 9 S 9 9 u.^ si?" \< 









e 



Apa akuwalimbikitsa zakusamuka ndi kuwauza kuti kumene akupitako 
akapeza bwino. Akuwalimbikitsanso okalamba ndi odwala kuti asamuke. 
Ngati atafera panjira kuwerengedwa kuti adasamukabe ndipo adzapeza 
mphoto yonga yayemwe adasamuka nkukakhala ku Madina pamodzi ndi 
Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndi kukathandiza kukamenya 
nkhondo yoteteza Chisilamu kwa adani. Ndi chimodzomodzi munthu akapita 
ku Makka kukachita Haji ndipo nkumwalira Hajiyo asanachite, kapena 
asanamalize zina zofunika pa Haji, kwa Mulungu amamuwerenga kuti wachita 
mapemphero a Haji. Komabe abale ake akhoza kukamchitiranso 
mapemphero a Haji. 

2 Pamene Asilamu adawalamulira zakusamuka, adawafupikitsira Swala 
chifukwa chamavuto am'njira monga kuti (a) Swala zokhala ndi raka zinayi 
akhoza kuziswali ndi raka ziwiriziwiri. (b) Akhoza kuswali katatu kokha patsiku 
m'malo mwakasanu.lzi zili motere: Swala ya Azuhuri nkuiphatikiza pamodzi 
ndi swala ya Alasiri; kuzipemphera panthawi ya Azuhuri kapena 
kuzipemphera panthawi ya Alasiri. Swala ya Magharibi nkuipemphera 
pamodzi ndi swala ya Isha. Adzayamba kupemphera swala ya Magharibi raka 
zitatu kenako nkupemphera Isha raka ziwiri. Koma swala ya Asubuhi yokha 
njomwe imapempheredwa payokha ndiponso m'nthawi yake. Lamuloli 
analikhazikitsa pamene Asilamu adali ndi mantha ndi masautso am'njira. 
Ndipo Lidasiidwa momwemo losasinthika mpaka lero m'nthawi yomwe anthu 
akukwera galimoto, sitima ndi ndege. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



202 • *>■• 



t (tLmJI &jy 



^9 «. >< "\ >4'l> >fVf KH * - /m 



102. Ndipo ngati uli pamodzi 
(ndi Asilamu Pankhondo) 
ndikuwatsogolera Swala, Ndiye 
kuti gulu limodzi laiwo liimirire 
pamodzi ndi iwe ndikupemphera 
uku Atagwirizira zida zawo. Ndipo 
akamaliza kulambira kwawo, apite 
kumbuyo Kwanu(kuti 
akulondereni) ndipo lidze Gulu 
lina lomwe silidapemphere, 
lipemphere Nawe pamodzi; 
nawonso achenjere Ndikugwirizira 
zida zawo (nkupemphera), 
Chifukwa chakuti omwe 
sadakhulupirire akufuna kuti 
mutanyalanyaza zida zanu Ndi 
katundu wanu angokuukirani 
Nthawi imodzi. Koma sikulakwa 
kwainu Mutaika pansi zida zanu 
chifukwa Chakuvutitsidwa ndi 
mvula kapena ngati Mukudwala. 
Koma chenjeranaoni. Ndithudi 
Mulungu wawakonzera Chilango 
choyalutsa osakhulupirira. 1 



1 Swala yopemphera pagulu (jamaa) akuilimbikitsa zedi ngakhale kuti anthu 
ali pakati pankhondo. Ngati nthawi ya swala yakwana akuwauza kuti 
apemphere pagulu, koma asapemphere onse nthawi imodzi. Anthuwo 
agawike m'magulu awiri. Gulu lina liyang'ane komwe kuli adani, ndipo gulu 
lina likhale likupemphera pamodzi ndi (Imamu) mtsogoleri wawo. Komatu 
Swala akunkhondo amaswali raka ziwiriziwiri (Swala ililonse) kupatula Swala 
ya Magharibi. 

Tsono Imamu adzapemphera raka imodzi ndi awo omwe akupemphera nawo. 
Akaimirira kuti apemphere raka yachiwiri.aja omwe anali kupemphera naye 
aimilire ndi kupemphera raka yotsalayo mwachangu atamsiya imamu ali 
chiimirire. Ndipo apite kukalowa m'malo mwa anzawo omwe anali kuyang'ana 
komwe kuli adani. Tsono anzawowo adze nkudzapemphera ndi Imamu. 
Imamu akamaliza raka yake yachiwiri, iwo aimirire nkumaliza raka yawo 
yachiwiri. Komatu popempherapo zida zawo zikhale atazikoleka m'matupi 



Surat 4. An-Nisa' 



Juzu 5 



203 



o *j*-i 



1 i-L-Jt *JJ-" 



103. Mukamaliza Swala, 
pitirizani kumkumbukira Mulungu 
muli chiimire, chikhalire kapena 
Mutagona chammbali. Ngati 
mutapeza Chitetezo (chifukwa 
chakuti nkhondo palibe), 
Pempherani Swala zanu mwa 
chilamulo. Ndithudi, Swala 
ndilamulo lokhala ndi Nthawi kwa 
Asilamu. 1 

104. Ndipo musachite ulesi 
kutsata anthu (omwe Ndi adani), 
ngati mukumva kupweteka, 
Iwonso akumva kupweteka monga 
momwe inu Mukumvera 
kupweteka. Koma inu 
Mukuyembekezera kwa Mulungu 
Chomwe iwo sakuyembekezera. 
Ndipotu Mulungu Ngodziwa: 
Ngwanzeru. 2 

105. Ndithudi, 
takuvumbulutsira Buku Mwa 
choonadi kuti uweruzire pakati Pa 
anthu, monga momwe Mulungu 
Wakuphunzitsira. Ndipo usakhale 
Mtetezi wa achinyengo. 












mwawo pokhapokha ngati pali zifukwa zoikitsa zidazo pansi, zomwe azitchula 
kumapeto a ndimeyo 

1 Nkofunika nthawi zonse Msilamu kukumbukira Mulungu, osati panthawi 
yokha yopemphera koma amkumbukire m'chikhalidwe chake chonse ndi 
m'zochita zake zonse. Nthawi zonse apewe zomwe Mulungu waletsa ndi 
kutsata malamulo ake. 

2 Apa akuwalamula Asilamu kuti amenyere chipembedzo chawo ngakhale 
atapeza mavuto amtundumtundu. Chifukwa chomwe akupezera mavutowo 
nchachikulu zedi kuposa mavutowo palibe chinthu chachikulu chimene 
munthu angachipeze chabe popanda kuvutikira. 



Surat 4. An-Nisa' 



Juzu 5 



204 



o *£\ 



t tL^Jl djj**» 



106. Ndipo mpemphe 
chikhululuko Mulungu. Ndithudi, 
Mulungu Ngokhululuka kwabasi, 
Ngwachisoni chambiri. 

107. Ndipo usawaikile 
kumbuyo omwe Akudzichitira 
okha chinyengo. Mulungutu 
sakonda yemwe ali Wachinyengo, 
wamachimo. 

108. Akudzibisa kwa anthu 
(pochita za Machimo) koma 
sakuzibisa kwa Mulungu pomwe 
lye adali nawo Pamodzi pamene 
adali kupangana Usiku mawu 
osakondweretsa. Mulungutu 
Akudziwa bwinobwino zimene 
akuchita. 1 

109. Taonani! Inu ndi amene 
mwaayikira Kumbuyo pamoyo 
wapadziko lapansi. Kodi ndani 
amene adzatsutsana ndi Mulungu 
pa iwo tsiku lomaliza, Kapena 
ndani adzakhale Mtetezi wawo. 2 



\j&-gg&\&$bb$z$ 












1 Anthu achiphamaso amabisa zochita zawo kwa anthu kuti asazione. Koma 
salabadira kuonedwa ndi Mulungu pomwe Mulungu Njemwe adzawalipira. 
Pomwe Mulungu akudziwa zonse zimene zikuyenda m'mitima mwawo 
ndiponso akumva ndi kuziona zonse zimene akuchita. Kunali kofunika kwa 
iwo kumuopa Mulungu amene ali ndi mphamvu zochitira chilichonse chimene 
wafuna. 

2 M'ndime iyi Mulungu akuletsa anthu kuti asakhalire kumbuyo anthu oipa 
koma awaleke kuti awalange chifukwa chazoipa zawo ndi kuti amene 
adamuchitirapo zoipa apeze bwino muntima mwake. Choncho aweruzi amilandu 
achenjere kukhalira kumbuyo anthu oipa omwe ali nawo chitsimikizo kuti 
adachenjerera anzawo. Asaone ulemerero wamunthu mmene ulili ngakhale 
ali ndi chuma chotani. Koma m'malomwake akhalire kumbuyo amene ali 
oponderezedwa. Akatero adzapeza mphoto yomwe Mulungu walonjeza 
chifukwa chakusonyeza choonadi poyera. Aweruzi akagwira njira imeneyi 
ndiye kuti adzapambana pano padziko lapansi mpaka patsiku lachiweruzo. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



205 



*jJU| 



t *L«%Jl QjJ~* 



110. Ndipo amene angachite 
choipa (povutitsa Ena), kapena 
kudzichitira yekha zoipa Ndipo 
kenako nkupempha chikhululuko 
kwa Mulungu, adzampeza 
Mulungu ali Wokhululuka, 
Kwabasi,Wachisoni kwambiri. 1 

111. Ndipo amene angachite 
tchimo, ndiye kuti Akudzichitira 
yekha. Mulungu Ngodziwa, 
Ngwanzeru zakuya. 2 

112. Ndipo amene angachite 
cholakwa (Chaching'ono) kapena 
tchimo (Lalikulu) kenako 
nkumponyera Nalo yemwe 
sadalakwe momunamizira, 
Ndithudi, wasenza bodza lalikulu 
Lamkunkhuniza ndi uchimo 
woonekera. 

113. Ndipo pakadapanda 
ubwino wa Mulungu ndi chisoni 
chake paiwe, Ndithudi, gulu 
limodzi laiwo Likadalinga 



[0 9 ^ 






foi'^/fl't^V. 









Mulungu akuwalimbikitsa ochimwa: (a) Kuti atembenukire kwa lye 
mwachangu ndi kusiya zimene akuchitazo. (b) Atsimikize mumtima kuti 
sadzachitanso uchimowo. (c) Adandaule pauchimo umene adauchitawo. (d) 
Awabwezere eni zinthu zomwe adazitenga mwachinyengo. (e) Akawapemphe 
kuti awakhululukire. Akakwaniritsa zonsezi ndiye kuti kulapa kwawo Mulungu 
akuvomera. 

2 M'ndime iyi akuti munthu wochitira anthu anzake zoipa, akudzipha yekha 
pakuti Mulungu sadzamleka koma amkhaulitsa pompano padziko lapansi 
kapena pakutha kwadziko. 

3 Pali anthu ena amene amaukwera uchimo. Kenako nkumanamizira wina 
wake. Munthu wamakhalidwe awa, chiweruzo chake chidzakhala choopsa 
tsiku lomaliza, ngakhale wadzipulumutsa pano padziko lapansi chifukwa 
chakuthyathyalika kwake. Kapena pompano padziko lapansi amachiona 
chomwe chinameta nkhanga mpala. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



206 * *>» 



i tL-Jl Sjj-*» 









kukusokeretsa. Ndipo Iwo palibe 
yemwe akadamsokeretsa Koma 
iwo okha basi. Ndipo sangathe 
Kukuvutitsa ndi chilichonse. Ndipo 
Mulungu wakuvumbulutsira 
Buku, Kudzanso luntha. Ndipo 
wakuphunzitsa Zomwe sudali 
kuzidziwa. Ndipo ubwino wa 
Mulungu umene uli paiwe 
ngwaukulu zedi. 

114. Palibe ubwino m'zambiri 
zimene Akunong'onezana kupatula 
amene Akulamulira ena kupereka 
sadaka, Kapena kuchita zabwino, 
kapena Kuyanjanitsa pakati pa 
anthu (Pakunong'onezana mawu). 
Amene Angachite 
zimenezi,chifukwa chofuna 
Chiyanjo cha Mulungu, 
tidzampatsa Malipiro aakulu. 

115. Ndipo amene anyoza 
Mtumiki Pambuyo pomuonekera 
chiongoko Nkutsata njira 
yosakhala ya Asilamu, 
Timtembenuzira kumene 
Watembenukira mwini wakeko. 
Ndipo tidzamulowetsa ku 
Jahanama. Taonani kuipa malo 
ofikira. 



Apa Mulungu akunena kuti palibe chisomo chimene Mulungu wapatsa 
munthu chachikulu ndi chopindulitsa kuposa luntha. Chilichonse chabwino 
chapadziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro chimapezeka chifukwa cha 
kudziwa zinthu. Qur'an yonse ndi hadisi za Mtumiki zikulimbikitsa 
zakufunafuna luntha lodziwira zinthu zakuti zimkonzere munthu zadziko 
lapansi ndi za tsiku lachimaliziro, kotero kuti Qur'an ndi hadisizo zikunena kuti 
munthu apite kunja kunka nafunafuna maphunziro. 






Surat4. An-Nisa 9 Juzu 5 



207 



*jJrl 



t s-L-Jl £jj-" 



116. Ndithudi, Mulungu 
sakhululuka (utchimo) 
Womphatikiza ndi chinthu china, 
(pochiyesa Kuti ndi mnzake wa 
Mulungu). Koma lye 
Amakhululukira matchimo ena 
omwe sali Amenewo kwa yemwe 
wamfuna. Ndipo yemwe 
Angamphatikize Mulungu (ndi 
milungu yabodza), Ndithudi, 
wasokera; kusokera konka nako 
kutali (Ndi njira yachoonadi). 

117. Sapembedza Mulungu 
koma Mafano achikazi, ndiponso 
Sapembedza china koma satana 
Wonyoza (wamatchimo) 

118. (Yemwe) Mulungu 
adamtemberera. Ndipo lye 
(Satana) adati (kwa Mulungu): 
"Ndithudi, ndikadzipezera gawo 
lodziwika Mwa akapolo anu;" 1 

119. "Ndikawasokeretsa ndi 
kuwapatsa Ziyembekezo (zabodza) 
ndithu Ndikawalamula kuti 
azikadula makutu A ziweto, ndipo 
ndikawalamulanso Kuti 
azikasintha chilengedwe cha 
Mulungu." Ndipo amene 
angamulole Satana kukhala 



9. 9 *" a S\ ' 9 u" 9 1 9 •* V» 'i» I £ I 






9 W' >&' 99%"*'i\'99<i% .Vftf 






Iblis pamene adampirikitsa kumwamba iye adauza Mulungu kuti 
akazikometsera zolengedwa zake matchimo. Mulungu adamuuza kuti 
sangathe kuzisokereza mwamphamvu, mozikakamiza, zifune zisafune. 
Aljyense amene akamtsata ndiye kuti akamtsata mwachifuniro chake. 
Sikuti mogonjetsedwa ndi mphamvu za Satana kotero kuti iye sangathe 
kulimbana naye iyayi. Satana alibe mphamvu zokakamizira anthu. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 5 



208 



*j*-\ 



t s-l^Jl ^J-** 



mtetezi wake kusiya 
Mulungu,ndiye kuti wataika 
koonekera. l 

120. (Satana) akuwalonjeza 
ndikuwapatsa chiyembekezo 
(Pazinthu zomwe sizingachitike). 
Ndithudi, Satana sawalonjeza 
china koma Chinyengo basi. 

121. Iwowo malo awo ndiku 
Jahanama;ndipo sadzapeza 
Pothawira kutuluka mmenemo. 

122. Ndipo omwe akhulupirira 
ndi Kumachita zabwino, 
tidzawalowetsa Ku minda yomwe 
pansi ndi patsogolo Pake mitsinje 
ikuyenda. Adzakhala M'menemo 
muyaya. Hi ndilonjezo Loona la 
Mulungu. Kodi ndani woona 
Ponena kuposa Mulungu? 

123. (Kulowa ku Munda 
Wamtendere) sikuli Pakukhumba 
kwanu ngakhalenso pakukhumba 
Kwa anthu a Buku. (Koma kuli 






^^^W 



(©Lag^l^ 









1 Apa akutchula zlna mwazinthu zomwe Satana adzasokeretsa nazo anthu: 
(1) Kukhala ndi chiyembekezo choti Mulungu adzawakhululukira pakuti iye 
ngokhululuka, Ngwachifundo. (2) Kuti ukachita zakutizakuti kapena 
ukawerenga duwa yakutiyakuti machimo ako onse adzakufafanizira ngakhale 
kuti udakwatula zinthu za anthu. (3) Kuti wolemekezeka uje adzatiwombola 
ngati tilumikizana naye. (4) Kuti mneneri wakutiwakuti adzaitana omtsatira ake 
kuti akalowe kumunda wamtendere. (5) Kuti Mtumiki sadzakhala wokondwa 
kuona anthu ake akuponyedwa kumoto. (6) Kukhala ndi chiyembekezo choti 
ngati munthu ndiwe Msilamu basi sukalowa ku Jahanama. 
Ndipo Satanayu amanyenganso Akhrisitu kuti ngati akhulupirira Yesu basi 
sakalowa kumoto. Ndipo Ayuda amawauzanso chimodzimodzi kuti ngati 
akhulupirira m'chipembedzo cha chiyuda sakalowa kumoto. Nawonso 
opembedza moto ndi Abudha amawauzanso chimodzimodzi kuti ngati atsata 
chibudha basi apulumuka. 



Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 209 ° *>' 



t s-L-Jl ^JJ-" 



pakulungama Ndi kuchita zomwe 
Mulungu afuna). Amene angachite 
choipa, adzalipidwa (nacho) Ndipo 
sadzapeza mtetezi Ngakhale 
mpulumutsi kupatula Mulungu. 

124. Ndipo amene angachite 
ntchito zabwino, mwamuna 
Kapena mkazi, pomwe iye ali 
wokhulupirira, Iwo ndi amene 
adzalowa kumunda Wamtendere. 
Ndipo sadzaponderezedwa 
chilichonse choipa, Ngakhale 
chochepetsetsa kwambiri ngati 
Kamphako ka nthangala ya tende 

125. Kodi ndani yemwe ali ndi 
chipembedzo Chabwino choposa 
yemwe walunjika Nkhope yake 
kwa Mulungu, iye ali Wabwino 
ndipo akutsata njira ya Ibrahim 
Woona pa chikhulupiriro. Ndipo 
Mulungu Adasankha Ibrahim 
kukhala bwenzi 

126. Ndipo zonse zakumwamba 
ndipansi nza Mulungu; ndipo 
Mulungu ndi amene Wazungulira 
chinthu chilichonse kuchidziwa. 

127. Ndipo akukufunsa zomwe 
zikukhudza Azimayi nena: 
"Mulungu akukuuzani Nkhani za 
iwo ndi zomwe zikuwerengedwa 
Kwa inu m'Buku (ili) zaakazi 
amasiye Omwe simukuwapatsa 
(chiwongo chawo) Chomwe 
chidalamulidwa kwa iwo, 









"W*} A* - ' <y*3 ^ii (y—»-l fcr«j 






Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



210 • «■>■• 



£ frU*Ujl CjJ-"' 



komabe Mukufuna kuwakwatira 
ndi za ana omwe Ali ofooka ndi 
oponderezedwa; ndipo 
(Akukuuzani) kuti limbikirani 
kuwayang'anira Ana amasiye 
mwachilungamo. Ndipo Chabwino 
chilichonse chimene muchita, 
Mulungu akuchidziwa. ' 

128, Ndipo ngati mkazi ataona 
kuti ndi Mwamuna wake 
akukanganakangana Ndi 
kupatulana, palibe kulakwa pa iwo 
Kuyanjana pakati pawo 
mwachimvano. Ndipo chimvano 
ndichabwino. (Munthu Aliyense 
amaumirira chimene afuna). 
Chifukwa chakuti mitima ya anthu 
imaumirira Umbombo. Koma ngati 
muchita zabwino Ndi kuopa 
Mulungu, ndithudi, Mulungu 
Ngodziwa nkhani zanu zonse 
zomwe muchita. 

129. Ndipo inu simungathe 
kuchita chilungamo (Chenicheni) 
pakati pa akazi ngakhale 
Mutayesetsa chotani. Koma 
musapendekere (Mbali imodzi); 
kupendekera kwathunthu kotero 
Kuti nkumusiya (yemwe 
simukumfunayo) ngati Kuti 
wapachikidwa (osadziwika kuti 
ngokwatiwa Kapena ayi). Ndipo 
ngati mutayanjana ndi Kuopa 















e^l^w^SGW 



1 Mukuuzidwa nkhanizi zomwe akuwerengerani mu ndime ya 2 ndi 12 M'sura 
yomweyi . 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



211 • »>» 



t $.L*Jt *J>^ 



Mulungu (zingakhale bwino). 
Ndithudi, Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachisoni Zedi. 

130. Koma ngati atalekana, 
Mulungu angalemeretse Aliyense 
waiwo kuchokera m'zabwino Zake 
Zochuluka ndipo Mulungu ali nazo 
zambiri, Ngwanzeru zakuya. 

131. Zonse zakumwamba ndi 
pansi nza Mulungu. Ndithudi, 
tidawalangiza omwe Adapatsidwa 
buku patsogolo panu ndi Inunso 
kuti muopeni Mulungu. Koma 
ngati mungakane, ndithudi, zonse 
Zakumwamba ndi pansi nza 
Mulungu. Ndipo Mulungu 
Ngokhupuka kwabasi 
Wotamandidwa. 

132. Zonse zakumwamba ndi 
pansi nza Mulungu; ndipo 
Mulungu akukwana Kukhala 
mtetezi (kwa anthu Ake). 

133. Ngati atafuna, 
akuchotsani, Inu anthu, ndi 
kubweretsa ena. Ndipo Mulungu 
ali wokhoza Pazimenezo. 

134. Amene afuna mphoto 
yadziko lapansi, (Afunefune kwa 
Mulungu). Kwa Mulungu 
Ndikumene kuli mphoto yapadziko 
lapansi ndi Ya tsiku lomaliza. 
Ndipo Mulungu Ngwakumva, 
Ngopenya. 












Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



212 



*jJU| 



i $.L*Jl ojj-** 



135. "E inu amene 
mwakhulupirira! Khalani Oimiritsa 
chilungamo, opereka umboni 
Chifukwa cha Mulungu; ngakhale 
kuti Ubwere ndi masautso kwa inu, 
kapena kwa Makolo anu, kapena 
kwa abale anu, ngakhale Ali 
olemera kapena osauka, 
(musayang'ane Zimenezo). 
Mulungu ndiye woyenera 
kuyang'ana Za awiriwo. Choncho 
musatsate zilakolako Ndi kusiya 
chilungamo. Ngati mukhotetsa 
(Umboni), kapena kupewa 
(kupereka Umboni) ndithudi 
nkhani zonse zomwe Mukuchita 
Mulungu akuzidziwa. 

136. "E inu amene 
mwakhulupirira! Khulupirirani 
Mulungu ndi Mtumiki Wake, ndi 
Buku lomwe analivumbulutsa Pa 
Mtumiki Wake, ndi mabuku 
Omwe adawavumbulutsa kale. 
Ndipo amene akane Mulungu, 
Angelo Ake, mabuku Ake, atumiki 
Ake ndi tsiku lomaliza,ndiye kuti 
wasokera; Kusokera konkera nako 
kutali. 

137. Ndithudi, amene 
adakhulupirira, Kenako 
nkusakhulupirira, 
Nadzakhulupiriranso, kenako 
Nkusakhulupiriranso, naonjezera 
Kusakhulupirira, Mulungu 
Sadzawakhululukira, ndipo 









$&&%&&*&$& 

$$*&#&$&&& 

&%?$&$& 



Surat4. An-Nisa' Juzu 5 



213 



o *>i 



£ *L*Jt Sjj-*' 



Sadzawawongolera m'njira 
(yabwino) 

138. Auze Amunafikina 
(Achiphamaso) kuti Adzapeza 
chilango chowawa; 

139. (Achiphamaso) omwe 
amaachita Osakhulupirira kukhala 
abwenzi Awo kusiya Asilamu. 
Kodi Akufuna kupeza ulemerero 
kwa iwo? Ndithudi ulemerero 
wonse ngwa Mulungu; (suli 
m'manja mwa anthu). 

140. Ndithudi lye 
wakuvumbulutsirani m'Buku (ili) 
kuti Mukamva maaya (ndime) a 
Mulungu akukanidwa ndi 
Kuchitiridwa chipongwe, 
musakhale pamodzi nawo Mpaka 
alowe m'zokamba zina. (Ngati 
mutakhala Nawo) ndiye kuti 
mukhala chimodzimodzi ndi iwo. 
Ndithudi, Mulungu 
adzawasonkhanitsa Achiphamaso 
ndi osakhulupirira onse m'moto 
wa Jahanama. 

141. (A chiphamaso) omwe 
akukuyembekezerani (kuti Mavuto 
akugwereni), ngati mutapeza 
kupambana Kochokera kwa 
Mulungu, amakuuzani "Kodi 
sitidali nanu limodzi?" Koma ngati 
Osakhulupirira atapeza gawo 
(lopambana), Amanena (kwa 
osakhulupirira;) "Kodi 
Sitidayandikire kukugonjetsani 



©^l^&t^!^ 



■U# 















Surat 4. An-Nisa' Juzu 5 



214 



a *jJUl 



t $.L*Jl <*JJ~** 



pamene Tidali M'gulu lankhondo 
la Asilamu koma 

Timakutsekerezani kwa Asilamu?" 
Koma Mulungu adzaweruza pakati 
Panu tsiku lachiweruzo. Ndipo 
Mulungu Sangawaikire njira 
osakhulupirira pa Asilamu (kuti 
awagonjetse kotheratu). 

142. Ndithu, achiphamaso 
akufuna kunyenga Mulungu Koma 
lye awalanga (chifukwa cha 
chinyengo Chawocho). Ndipo 
akaimirira kupemphera Swala, 
amaimirira mwaulesi 
ndikungoonetsa anthu (Kuti 
akupemphera). Ndipo satchula 
Mulungu Koma pang'ono pokha. 

143. Akungoyendayenda pakati 
pa awa ndi awa (Pakati pa Asilamu 
ndi osakhulupirira). Iwo Sali mbali 
iyi kapena mbali inayo. Ndipo 
Amene Mulungu wamlekerera kuti 
asokere Sungampezere njira 
yolungama. 

144. "E inu amene 
mwakhulupirira! Musawachite 
osakhulupilira kukhala Abwenzi 
ami kusiya okhulupirira (Asilamu) 
kodi mukufuna Kuti Mulungu 
akhale ndi Mtsutso woonekera 
painu (Kuti ndinu oyipa?)" 

145. Ndithu achiphamaso 
Adzakhala pansi penipeni Pamoto; 
ndipo sudzampeza Mthandizi 
woimira iwo. 












Surat4. An-Nisa' 



Juzu 6 



215 



1 *j*-» 



£ *L«Jt ^JJ- - 



146. Kupatula amene alapa 
(pambuyo pa Chiphamaso chawo); 
nakonza (makhalidwe Awo) 
nadziphatika kwa Mulungu; 
Namuyeretseranso Mulungu 
Nchipembedzo chawo. Choncho 
iwo Ali pamodzi ndi Asilamu. 
Ndipo Mulungu adzapatsa 
Asilamu malipiro akulu. 

147. Mulungu sangakulangeni 
ngati Mumthokoze ndi 
kumkhulupirira. Ndithudi, 
Mulungu Ngolandira Kuthokoza 
kwanu, ndiponso Ngodziwa. 

148. Mulungu sakonda 
kutulutsa Mawu ofalitsa kuipa 
(kwa anthu) Kupatula yekhayo 
wachitiridwa zoipa. Ndipo 
Mulungu Ngwakumva, 
Ngodziwa. 1 

149. Ngati mungaonetse 
chabwino, Kapena kuchibisa, 
kapena Kukhululukira zoipa, 
(zoterozo Ndizo zofunika) ndithu 
Mulungu Ngokhululuka ndiponso 
Ngokhoza. 

150. Ndithudi amene 
sakhulupirira Mulungu ndi 
Atumiki Ake, ndikufuna 
kumlekanitsa Mulungu Ndi 






@\$p£\ji\ 









1 Indedi, Mulungu sakonda anthu ofalitsa zoipa za anzawo popanda choipa 
chilichonse chimene awachitira. Koma munthu amene ena amchitira choipa 
akumlola kutchula kuipa komwe ena amchitira pokamnenera kwa muweruzi 
kuti muweruziyo amuthandize paamene amchitira zoipawo. Koma kulengeza 
kuipa kwa anthu ena nkosaloledwa m'chisilamu. Ndipo ndi utchimo waukulu. 



Surat4. An-NisS' 



Juzu 6 



216 1 *>■» 



t S-L*lJl 5jJ-*» 



atumiki Ake, ponena kuti: "Ena 
Tikuwakhulupirira, koma ena 
tikuwakana", ndipo Akufuna 
kugwira njira yapakati pa izi 
(Osati ya Chisilamu chenicheni 
kapenanso ya Anthu 
osakhulupirira). 1 

151. Iwo ndiwosakhulupirira 
Enieni. Ndipo osakhulupirira 
Tawakonzera chilango Choyalutsa. 

152. Ndipo amene akhulupirira 
Mulungu Ndi atumiki ake, 
nkusamulekanitsa Aliyense waiwo 
(koma nkwakhulupirira Onse), iwo 
adzawapatsa malipiro awo. Ndipo 
Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri, Wachisoni zedi. 

153. Anthu amene adapatsidwa 
Buku (Ayuda) akukupempha (Iwe 
Mtumiki) kuti uwatsitsire Buku 
kuchokera Kumwamba. Ndithudi, 
adampemphanso Musa zazikulu 
Kuposa zimenezi pomwe adati: 
"Tiwonetse Mulungu Poyera". 
Ndipo udawagwira moto 
wamphenzi (umene Udachotsa 



* A 9 ' 



J 






99 9 ~%* IV *'e* < 9 *u 9S<? V 



Aliyense mwa anthu yemwe Mulungu wamuvomereza kuti ndi mtumiki 
Wake, ndipo iwe nkukana kumkhulupirira, monga Ayuda mmene amamkanira 
Mneneri Yesu, ndi Akhrisitu mmene amamkanira Mneneri Muhammad (SAW), 
kutereko nkusakhulupirira Mulungu. Asilamu amavomereza Aneneri onse 
oona amene adadza Muhammad (SAW) asadabadwe. Asilamu akuvomereza 
aneneri onse monga momwe Mulungu wafotokozera n'Qur'an. Ndipo 
savomereza omwe Mulungu sadawavomereze kuti ndi Aneneri ake. Oterewa 
ndi amene akunama kuti adapatsidwa uneneri pambuyo pa Mneneri 
Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) monga Mirza Gulam 
Ahmad ndi Bahai. Amene akukhulupirira amenewa ndiye kuti ngopandukira 
Mulungu. Tero tichenjere ndiudyerekezi wa Akadiani ndi Abahai ndi ena otere. 



Surat4. An-Nisa' Juzu 6 



217 



% frjA-i 



t ti—Ji ojj— * 



miyoyo yawo chifukwa 
chakusakhulupirira Kwawo. 
Zitatero Mulungu adawapatsa 
moyo kachiwiri). Ndipo kenako 
iwo adapanga thole (mwana 
wang'o mbe Monga Mulungu 
wawo) pambuyo powafikira 
Zisonyezo zoonekera. Koma 
tidawakhululukira Zimenezo, 
ndipo tidampatsa Musa zisonyezo 
Zooneka. 1 

154. Ndipo tidatukula phiri 
pamwamba pawo (Ayudawo) 
polandira pangano lawo; Tidati 
kwa iwo: "Lowani pachipata 
(Chadziko ili la Shamu) 
mutawerama". Tidatinso kwa iwo: 
"Musalumphe Malire (pochita 
usodzi) tsiku la Sabata". Ndipo 
tidalandira kwaiwo Pangano 
lokhwima. 



®\£^^)al£ 






1 Ayuda adauza mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
kuti sangakhulupirire pokhapokha amuone akukwera kumwamba popanda 
kugwirira chilichonse ndi kubwera pansi pano Buku lili m'manja mwake 
mutalembedwa umboni wa Mulungu woti iye Muhammad ndi Mtumiki 
Wakedi. Ndipo Mulungu akuti makhalidwe otsutsana ndi Aneneri siachilendo 
kwa Ayuda. Ndipo Musa atalephera kuchita zimenezo adamuda. Tero 
adapanga fano (lamwana wang'ombe 'thole') naliyesa Mulungu wawo. 

2 (Ndime 154-6) Mulungu akupitiriza kufotokoza zoipa zawo. Ndipo zina 
mwaizo ndiizi: 

(a) Adakana kutsatira malamulo am'Taurat. Ndipo Mulungu adazula phiri 
naliimitsa pamwamba pamitu yawo nawauza kuti: "Ngati simulola kulonjeza 
kuti mdzatsata zomwe zili m'Taurat, likusinjani phiri ili. 

(b) Adakana kulowera pachipata kudziko la Shamu Kenani monga momwe 
Mulungu adawalangizira. Ndipo adalowa monga momwe iwo amafunira. 
Shamu ndi dziko lomwe Mulungu adawapatsa kuti akalowemo ndi kukhazikika 
pambuyo posamuka ku Eguputo (Egypt). Koma iwo sadathokoze chisomochi 
potsata zomwe Mulungu adawauza. 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 6 



218 1 ►>■• 



£ *L«Jl Sjj** 



155. Choncho (tidawalanga) 
chifukwa chakuswa Mapangano 
awo, ndi kukana kwawo zisonyezo 
Za Mulungu, ndi kupha kwawo 
aneneri popanda Choonadi, ndi 
kunena kwawo kwakuti, "Mitima 
yathu yakutidwa (siingathe 
kuzindikira Zomwe ukunena iwe 
Muhammad {SAW})". ( Ai, 
Siinakutidwe ndi chilichonse), 
Koma Mulungu Waidinda zidindo 
chifukwa chakusakhulupirira 
Kwawo; tero sakhulupirira koma 
pang'ono pokha. 

156. Chifukwa 
chakusakhulupirira kwawo ndi 
Kumnamizira kwawo Maria bodza 
lalikulu (Kuti wabala Yesu m'njira 
yachiwerewere); 






^mzK^stfb 



(c) Pambuyo polowa m'dzikolo adawauza kuti alemekeze tsiku la Sabata kuti 
likhale tsiku lamapemphero okhaokha. Lisakhale tsiku logwira ntchito. Koma 
iwo adachitachita ndale zawo mpaka lidasanduka tsiku logwira ntchito. 

(d) Ena mwa aneneri awo pamene adawaletsa iwo machitidwe amenewa 
mwaukali.adawapha. 

(e) Mneneri Muhammad pamene adawafotokozera zizindikiro zomwe zinali 
m'mabuku mwawo zimene zimasonyeza utumiki wake sadamulabadire. 
"Mitima yathu yakutidwa. Siikumvetsa chilichonse chimene ukunena". 

(0 Mneneri Yesu pamene adawafotokozera za utumiki wake ndi 
kuwasonyeza zozizwitsa ndi zonse zomwe zidachitika m'kubadwa kwake, iwo 
adati Mayi Maria adatenga pakati m'njira yachiwerewere pomwe iwo 
amadziwa kuti akungonama. 

(g) Adakonza chiwembu kuti aphe Yesu. Koma Mulungu adachiononga 
chiwembu chawocho pomuveka munthu wina nkhope ya Yesu amene adali 
wamkulu wawo yemwe ankafunisitsa kupha Yesu. Tero adampachika 
mnzawoyo pamtanda. Pambuyo pake, akuluakulu aChiyuda adazindikira 
zonse zomwe zidachitikazi. Ndipo adangonyozera ngati kuti sichidachitike 
chilichonse chododometsa chifukwa choopa kuti anthu angawaukire. 
M'malomwake ankangodzidzudzula okha m'mtima mwawo. 



Siirat 4. An-Nisa' Juzu 6 | 219 t ^ 



t *.L-*Jl SjJ-*' 



157. Ndikulankhula kwawo 
(kwakuti) "Ife tamupha Mesiya 
Yesu mwana wa Maria, Mtumiki 
wa Mulungu; Koma sadamuphe 
ndipo sadampachike Pamtanda. 
Koma adasokonezedwa (ndi 
munthu Wina namuganizira kuti 
ndi Yesu). Ndithudi, Amene 
akutsutsana pankhani 
(yakuphedwa kwake) Ali 
m'chikaiko ndi kuphedwa kwake; 
alibe kudziwa Kotsimikizika, 
koma akungotsatira 
Zongoganizira. Ndithudi, 
sadamuphe. 

158. Koma Mulungu 
adamkweza Kwa lye ndipo 
Mulungu Ndimwini mphamvu 
zoposa, Ngwanzeru zakuya. 

159. Palibe aliyense mwa anthu 
omwe adapatsidwa Buku (Ayuda 
ndi Akhrisitu amene Amamwalira 
asanazindikire za momwe Yesu 
Adalili); koma amamzindikira 
ndithu (kuti Sadali Mulungu) 
patangotsala pang'ono Kumfikira 
imfa yake. (Nayenso Yesu) pa 
Tsiku lachiweruzo adzaikira 
umboni paiwo (Kuti iye adali 
chabe kapolo wa Mulungu). 

160. Chifukwa chakuchita 
kwawo zoipa, awo Ayuda, 
tidaletsa kwa iwo zinthu zabwino 
(Zakudya)zomwe zidali 






e^SM6«ri*«a^ 









Surat 4. An-Nisa' Juzu 6 



220 



1 *>» 



t s-L-Jl 0jj«*» 



zovomerezeka kwa iwo; Ndiponso 
chifukwa chakutsekereza kwawo 
Anthu ambiri kuyenda panjira ya 
Mulungu. 

161. Ndi kudya kwawo riba 
(katapira) pomwe Adaletsedwa 
kuti asadye; ndiponso chifukwa 
Chakudya kwawo chuma cha 
anthu Mwachinyengo. Ndipo 
osakhulupirira mwa Iwo 
tawakonzera chilango chopweteka. 

162. Koma mwaiwo amene 
azama pamaphunziro, Ndi Asilamu 
(onsewo) akukhulupirira zimene 
Zavumbulutsidwa kwa iwe ndi 
zimene Zidavumbulutsidwa 
patsogolo pako. Ndipo omwe 
akupitiriza Kupemphera swala, 
ndikupereka Zakati, ndi 
kukhulupirira mwa Mulungu ndi 
tsiku lomaliza, Iwo tidzawapatsa 
malipiro akulu. 

163. Ndithudi, 
takuvumbulutsira (chivumbulutso) 
Monga momwe 

tidamuvumbulutsira Nuhu (Nowa) 
ndi aneneri amene anadza 
pambuyo pake. Ndipo 
tidavumbulutsiranso Ibrahim, 
Ismael, Ishaaq, Yakub ndi 
mbumba yake. Ndipo 
(tidavumbulutsiranso) Isa, Ayub, 
Yunusu, Haarun ndi Sulaiman, 
ndipo Daudi Tidampatsa Zabur 
(Masalimo). 



©j^ 









hV*'-^ 






Surat4. An-Nisa' 



Juzu 6 



221 



n *>» 



i *.L«Ji 5jj-*> 



164. Ndipo (tidavumbulutsanso 
chivumbulutso) Kwa aneneri 
omwe takusimbira kale (nkhani 
Zawo) ndi aneneri ena omwe 
sitinakusimbire (Nkhani zawo); 
ndipo Mulungu adayankhula Ndi 
Musa mwachindunji. 

165. (I wo ndi) aneneri omwe 
adauza nkhani zabwino (Kwa 
anthu abwino) ndi kuwachenjeza 
(oipa) Kuti anthu asadzakhale ndi 
mtsutso pa Mulungu Pambuyo pa 
(kudza kwa) aneneriwa. Ndipo 
Mulungu Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 

166. Koma Mulungu akuikira 
umboni zimene Wakuvumbulutsira 
(kuti nzoona) Adavumbulutsa 
mwanzeru Yake. Nawonso angelo 
akuikira umboni. Ndipo Mulungu 
akukwana kukhala mboni. 

167. Ndithu, amene 
sadakhulupirire, naletsa (Anthu) 
kuyenda panjira ya Mulungu, 
Ndithudi, asokera; kusokera 
Komka nako kutali. 

168. Ndithudi, amene 
sadakhulupirire, Namachita zoipa, 
kwa Mulungu Sipadzakhala 
kuwakhululukira Ngakhale 
kuwatsogolera njira. 

169. Kupatula njira yomka ku 
Jahanama Mmenemo akakhala 



9 Iff 9)\* '<>*&& 9*' 















Surat4. An-Nisa' 



Juzu 6 



222 1 *>» 



i tt~Jl Sjj-* 



muyaya. Ndipo zimenezo 
nzopepuka Kwa Mulungu. 

170. E inu anthu! Mtumiki 
(Muhammad{SAW}) 
Wakudzerani ndi choonadi 
Chochokera kwa Mbuye wanu. 
Choncho Khulupilirani; ndi bwino 
kwa inu kutero. Koma ngati 
mukana, (dziwani kuti) zonse 
Zakumwamba ndi zapansi nza 
Mulungu; (Palibe chomwe 
angaluze Pakusakhuluprira 
kwanu). Ndipo Mulungu 
Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru 
zakuya. 

171. E inu anthu a Buku! 
Musamalumphe malire 
Pachipembedzo chanu. Ndipo 
musamnenere Mulungu koma 
zowona (zokhazokha) Ndithu 
Mesiya Yesu mwana Wa Maria, 
ndi mtumiki wa Mulungu 
(ndiponso ndi munthu 
wolengedwa) Ndi liwu lake 
lomwe adaliponya kwa Maria 
Ndiponso (ali) ndi mzimu 
wochokera kwa lye (Mulungu, 
monga Mizimu ina yonse 
Imachokera kwa lye). Choncho 
Khulupirirani Mulungu ndi 
atumiki Ake. Musamanene "Utatu 
wa Mulungu;" siyani, 
(Zikhululupiriro za utatu wa 
Mulungu), kutero Ndibwino kwa 
inu. Ndithudi, Mulungu ndi 









Surat4. An-Nisa' Juzu 6 



223 



n frjJrt 



£ fLwJl 5jJ~J 



Mulungu m'modzi (basi). 
Ulemerero wake ngotukuka kutali 
ndi kukhala Ndi mwana. Nzake 
zonse zakumwamba ndi pansi. 
Ndipo Mulungu ndiMtetezi 
Wokwanira. 

172. Mesiya (Mneneri Yesu) 
sangaone kunyozeka Kukhala 
kapolo wa Mulungu ngakhalenso 
Angelo oyandikitsidwa (kwa 
Mulungu). Amene angaone 
kunyozeka paukapolo wake Kwa 
Mulungu nazitukumula, onse 
Adzawasonkhanitsa kwa lye 
(ndipo Kenako nkuwalonga 
kung'anjo ya moto). 

173. Koma amene 
adamkhulupirira (Yesuyo) Ndi 
kuchita zabwino Adzawapatsa 
malipiro ao bwinobwino ndi 
Kuwaonjezera ndi zabwino zake. 
Koma amene Adaona kunyozeka 
(pokhala kapolo wa Mulungu) 
nadzitukumula,adzaalanga 
Ndichilango chowawa; ndipo 
sadzapeza bwenzi Ngakhale 
mtetezi kupatula Mulungu. 

174. E inu anthu! Ndithudi, 
Wakudzerani umboni Wochokera 
kwa Mbuye Wanu. Ndipo 
takuvumbulutsirani Kuunika 
koonekera poyera. 

175. Tsono amene akhulupilira 
Mulungu Ndi kudziphatika kwa 



} > »> ft* y,,'s ..sts 9' 









&\>,\p\&<£\w$ 



Surat4. An-Nisa' 



Juzu 6 



224 



t *>» 



t *L*Jl 5jJ-*» 



lye, Iwo adzawalowetsa ku 
Chifundo Chake ndi kuzaufulu 
Zake (mtendere) ndikuwatsogolera 
kwa lye panjira yoongoka. 

176. Akukufunsa (iwe Mneneri, 
za malamulo Achuma cha munthu 
yemwe wafa osasiya Mwana 
kapena kholo). Nena: "Mulungu 
Akukulamulani pazayemwe 
sadasiye mwana Ndi kholo (kuti) 
ngati munthu atamwalira Pomwe 
alibe mwana, koma ali ndi mlongo 
Wake, choncho (mlongo wakeyo) 
alandire Theka (Vi) ya zomwe 
wasiya (womwalirayo). Nayenso 
angalandire chuma (chamlongo 
wake) Ngati (womwalirayo) alibe 
mwana. Ngati Iwo ali (alongo) 
awiri, ndiye kuti Adzalandira 
zigawo ziwiri muzigawo zitatu 

C^Aj ) Za zomwe wasiya. Ngati ali 

pachibale amuna Ndi akazi, ndiye 
kuti mwamuna aliyense alandire 
Gawo lolingana ndi la akazi awiri. 
Umo Ndi momwe Mulungu 
akukufotokozerani (Malamulo 
Ake) mwatsatanetsatane kuti 
Musasokere. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa chilichonse 













Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



225 1 »>• 



OJjlit OjJ~» 



Surat Al-Ma'idah V 



C\--'^-. "±:y- 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. "E inu amene 
mwakhulupirira! Kwaniritsani 
Mapangano onse (omwe ali pakati 
panu ndi Anthu anzanu). 
Kwalolezedwa kwainu (kudya 
Nyama ya) ziweto (monga 
ngamira, ng'ombe Ndi mbuzi), 
kupatula chomwe mukuuzidwa 
(Kuti ncholetsedwa). Koma 
nkosaloledwa Kwainu kuchita 
ulenje mutalowa M'mapemphero a 
Haji, (kapena muli M'nthaka 
yopatulika ya ku Makka). 
Ndithudi, Mulungu akulamula 
chimene wafuna. 1 

2. "E inu amene 
mwakhulupirira! Musanyozere 
Kupatulika kwa zizindikiro za 
Mulungu (Kuchiyesa 
chosapatulika chomwe Mulungu 
Adachichita kukhala chopatulika; 
monga Kutuluka m'mapemphero a 
Haji usadakwaniritse), Kapena 






mm : . #- 



Q£ft$»lfc#2l^l, 



-^ 









1 Chisilamu chimalemekeza zinthu zogwirira ntchito ya chipembedzo, monga 
ziweto zimene amazitumiza ku Makka ncholinga choti akazizinge kumeneko 
monga sadaka yopereka konko. Ndipo anthu okachita mapemphero a Hajiwo, 
ziweto amaziveka zizindikiro zosonyeza kuti nziweto zomwe akukazipereka 
monga nsembe ku nyumba ya Mulungu mu mzinda wa Makka. Ndipo 
nyamazo zimakhala zopatulika. Choncho sibwino kuswa kupatulika kumeneku 
pozilanda mwachifwamba ndi kuzipha zisanafike pamalo pake poziphera. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



226 1 *>' 



o daJlit ojj^t 



kupatulika kwa mwezi wopatulika 
(Poyambitsa nkhondo mmenemo), 
Kapena (kupatulika kwa nyama 
zomwe Zatumizidwa ku Makka 
monga) nsembe Kapena (kuchotsa 
kupatulika Kwa) makoza (omwe 
nyamazo Zimavekedwa monga 
chizindikiro chosonyeza Kuti 
ndinsembe ya ku Makka), kapena 
(Kupatulika kwa) omwe akulinga 
kupita Kunyumba yopatulika (ku 
Makka), (omwe Akupita 
kumeneko) ndi cholinga 
chofunafuna Ubwino wa Mbuye 
wawo ndi chiyanjo Chake. Ngati 
Mutatuluka m'mapemphero Anu a 
Haji, mukhoza kuchita ulenje 
(ngati Mutafuna); Ndipo 
kusakuchititseni kuwada Anthu 
chifukwa chakuti adakutsekerezani 
kufika Ku Mzikiti wopatulika ( wa 
ku Makka) kuti Mulumphe malire. 
Pobwezera mtopola umene 
adakuchitirani) Koma thandizanani 
pazabwino ndikuopa (Mulungu); 
musathandizane pamachimo Ndi 
pa chidani. Ndipo muopeni 
Mulungu. Ndithu Mulungu 
Ngwaukali pokhaulitsa. 

3. Kwaletsedwa kwainu (kudya) 
chakufa chokha, Ndi liwende, ndi 
nyama yankhumba, ndi Chomwe 
chazingidwa m'dzina osati la 
Mulungu, ndi chomwe chafa ndi 
kubanika, Ndi chomwe chafa ndi 






M 









Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



227 1 *>■» 



dJJlil djj^ 



kumenyedwa, ndi Chimene chafa 
pakugwa (Kuchokera paphiri 
losongoka) ndi chimene Chafa 
polasidwa ndi nyanga 
(yachinzake), Ndi chomwe chafa 
pakujiwa ndi chilombo (Cha 
m'thengo) kupatula chomwe 
mwachipeza Chili moyobe, 
nkuchizinga. Ndi chimene 
Chazingidwa paguwa la mafano; 
ndiponso (Nkoletsedwa kwa inu) 
kufuna kudziwa zobisika Pochita 
maula. Zonsezi ndi uchimo. Lero 
amene sadakhulupirire ataya 
mtima (Zakugonjetsa) 
chipembedzo chanu. Choncho 
Musawaope, koma opani Ine. Lero 
Ndakukwaniritsirani chipembedzo 
chanu ndipo Ndakwaniritsa pa inu 
chisomo changa. Ndakusankhirani 
Chisilamu Kukhala chipembedzo 
chanu. Koma amene Wasimidwa 
chifukwa chanjala, popanda 
Kupendekera kumachimo, (nkudya 
zoletsedwazi, Palibe kanthu). 
Ndithu, Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri, Ngwachisoni. 1 



1 Apa atchulapo zinthu zoletsedwa kuzidya. Zinthuzi ndi izi> (a) Nyama imene 
yadzifera yokha. (b) Liwende (uwende). (c) Nyama yankhumba. (d) Nyama 
imene aizinga ndi cholinga china, osati ncholinga cha Mulungu monga:- 

(1) Nyama imene aizinga chifukwa chotsirika nyumba kuti ziwanda 
zisamavutitsemo. 

(2) Nyama imene aizinga pofuna kusangalatsa chiwanda cham'nyumba 
kapena cham'munda kuti chisangalale. Kapenanso pofuna kusangalatsa 
mzimu wa munthu wakufa kuti ngati sazinga nyama ndiye kuti uzivutitsa ana 
kapena anthu okhala panyumbapo. 

(3) Nyama imene aizinga pofuna kutsirika mudzi, kapena kuti chaka chino 
tikapanda kuzinga nyama kubwera matsoka akutiakuti. 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



228 1 *j*-» 



O OJJlil 



h** 



4. Akukufiinsa (Asilamu) 
chomwe chaloledwa Kwa inu 
(kudya). Nena: "Chaloledwa kwa 
inu Chilichonse chabwino. Ndi 
chimene chagwidwa Ndi nyama 
kapena mbalame zomwe 
Mwaziphunzitsa kusaka. 
Muziphunzitse zimene Mulungu 
wakuphunzitsani. Choncho idyani 
Chimene zakugwirirani, ndipo 
chitchulireni Dzina la Mulungu 
pochikhwirizira. Ndipo opani 
Mulungu. Ndithudi Mulungu 
Ngwachangu pakuwerengera. l 






(4) Nyama imene aizinga pofuna kutsirika ukwati kuti ulimbe kapena pofuna 
kutsirika yemwe wabwera kuulendo kuti asamlodze; 

(5) Nyama imene aizinga ncholinga choti akataye bwino maliro, ndi kuti 
mzimu wamalirowo usavutitse anthu pamudzi; Nyama zonse zimene 
zazingidwa ndizolinga monga izi tatchulazi, nzoletsedwa kuzidya. Ndipo 
kunena koti "Chimene chafa ndikumenyedwa ncholetsedwa koma 
pokhapokha mutachipeza chili moyobe nimuchizinga," tanthauzo lake nkuti 
nyama imene imadyedwa ngati itafa pazifukwa zina zilizonse, monga 
kugundidwa ndi galimoto ndi zina zotero ndipo nyamayo sinaferetu kotero 
kuti nkutheka kuizinga, nyama yotero njololedwa kuidya. 

1 Mbalame ndi nyama zimene zaloledwa kuzisaka mwaulenje kupyolera 
mwambalame kapena mwanyama zinzawo zomwe anaziphunzitsa kusaka, 
ndipo mbalamezo kapena nyamazo nkufa chifukwa chakulumidwa ndi mbalame 
kapena nyama zosakazo, zikuloledwa kuzidya ngakhale kuti sanaztzinge. 
Koma ngati atazipeza zikalipobe ndi moyo, azizinge. 

N B! Ndipo Mulungu nyama zomwe akuzilola kuti zizisaka zinzawo nzomwe 
zili ndimano akuthwa ndi zikhadabu zakuthwa ndipo zitalizitali. Chimodzimodzi 
ngati nyama ndi mbalame zitaphedwa ndi mipaliro kapena mikondo kotero 
kuti zaferatu, zikuloledwa kuzidya ngakhale kuti sadazizinge. Koma 
akazipeza zili moyobe, azizinge. Koma chida chimene chikupha mopsinja 
monga mwala ndi chibonga (chamtunga) kapenanso chida chokhala ndi 
moto, monga chipolopolo chamfuti, nyamayo kapena mbalameyo siiloledwa 
kudyedwa ndi mazingidwe oterowo. Koma chikapezeka kuti chili ndimoyobe 
ndipo nkuchizinga, pamenepo chikhala chololedwa kuchidya. Koma Mazihabi 
a Maalik akuti nchololedwanso kuchidya chinthu chimene chafa chifukwa 
cholasidwa ndi mwala kapena ndi chipolopolo chamfuti. Ndipo ganizoli 
akulitsata ambiri kuphatikizapo a Mazihabi a Shafi. Tsono chimene chili wajibu 
pozinga nyama pa Mazihabi a imam Shaafi ndichimodzi basi. Uku nkuchidula 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



229 1 *>» 



O OJU'lil 



Oj^ 



5. Lero mwaloledwa zonse 
zabwino ndi Chakudya cha omwe 
adapatsidwa Buku nchololedwa 
kwa inu, ndiponso Chakudya 
chanu nchololedwa Kwa iwo ndipo 
(mukuloledwa kuwakwatira) Akazi 
abwino a mwa Asilamu ndi akazi 
Abwino a mwa omwe adapatsidwa 
ma buku Kale, ngati mwawapatsa 
chiwongo Chawo m'njira yomanga 
nawo ukwati, Osati mochita 
chiwerewere, Osatinso mochita 
zibwenzi. Ndipo amene Akane 
kukhulupirira, ndiye kuti 
Yaonongeka ntchito yake; ndipo 
lye tsiku lomaliza adzakhala mwa 
oluza. l 









chinyamacho mwachangu njira imene imalowera chakudya ndi njira imene 
mpweya umalowera. Ndipo zina zotsatira pazimenezi ndisunna, monga.- 

(a) kuiyang'anitsa kuchibula (nyamayo) 

(b) kunena mawu akuti "Bismillah" 

(c) Mpeniwo ukhale wakuthwa 

(d) Kuigoneka pamalo posapweteka. Tsono kunena kwakuti "Mkazi 
sangazinge nyama ndi kutinso mpeni ukhale ndi chogwirira (chigumbu)," ndi 
mawu opanda pake. Msilamu aliyense, mwamuna ndi mkazi akhoza kuzinga 
ngati akudziwa. 

1 Chakudya chozingidwa sichingakhale chovomerezeka kwa Asilamu 
pokhapokha chitazingidwa ndi Asilamu. Izi zili ngati atatsatira malamulo 
talongosola aja pozinga, osati kupotokola khosi, kapena kumenya ndimyala 
kapena chibonga. 

Tsono chakudya chozingidwa nchovomerezeka kwa Msilamu kuchidya 
ngakhale chitakonzedwa ndi achikunja (akafiri) monga momwe zilili 
m'Mazihabi a Chisunni malinga ngati:- 

(a) simudaone kuti athiramo najisi (uve) 

(b) Sichili chakudya choletsedwa 

Nkovomerezeka kwa mwamuna wa Chisilamu kukwatira:- 

(a) Mkazi wa Chiyuda 

(b) Mkazi wa Ghikhrisitu ngati makolo awo adali Ayuda kapena Akhrisitu 
chisilamu chisanadze. 

N.B! Koma awa a Mishoni omwe alowa m'Chikhrisitu posachedwapa 
nkosaloledwa kuwakwatira pokhapokha atayamba alowa m'Chisilamu Tsono 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



230 1 *>» 



O dJJlll 



pj^-. 



6, "E inu amene 
mwakhulupirira! Pamene 
Mwaimilira kuti mukaswali, 
sambitsani Nkhope zanu, ndi 
manja anu mpaka Mmagongono; 
ndipo pakani madzi pamitu panu 
Ndi kusambitsa mapazi anu mpaka 
muakakolo. Ngati muli ndi janaba 
dziyeretseni (sambani Thupi 
lonse); Ndipo ngati muli odwala 
kapena Muli paulendo, kapena 
mmodzi Wanu wachokera 
kokadzithandiza Kapena 
mwakhalira limodzi ndi mkazi 
ndiye Simudapeze madzi, chitani 
Tayammamu Ndi dothi labwino 
ndipo pakani kunkhope Zanu ndi 
mmanja mwanu. Mulungu 
sakufuna Kukuvutitsani, koma 
akufuna kukuyeretsani Ndi 
kukwaniritsa chisomo chake painu 
Kuti muthokoze . 

7. Ndipo kumbukirani chisomo 
cha Mulungu Painu ndi pangano 
lake lomwe mudapangana Naye, 
pamene mudati: "Tamva; ndipo 



•f*"T <" \z,< \>* **??? 

»*/ 99} , 9 s ^*r< r^«»K \* * ' 






mkazi wa Chisilamu nkosaloledwa kukwatiwa ndi myuda kapena mkhrisitu. 
Ndipo apa apitirizanso machitidwe achiwerewere chomangira nyumba ndi 
chapatchire. Munthu akafuna kukwatira mkazi atsate mfundo zikudzazi kuti 
ukwati wakewo ukhale wovomerezeka pa malamulo a Chisilamu:- 

(a) Mkazi alole kukwatiwa ndi mwamunayo. 

(b) Myang'aniri wa wamkazi apereke kwa munthu chilolezo choti akwatitsire 
mkazi uja, kapena amkwatitse iye mwini pomuuza mkwati kuti "Ndakukwatitsa 
uje,mwana wauje". 

(c) Mkwati avomereze kuti: "Ndavomera kumkwatira uje, mwana wauje". 

(d) Pakhale anthu aamuna oikira umboni osachepera pa awiri. Anthuwo 
akhale aulemu wawo pamaso pa anthu. 



Siirat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



231 



n tjJt-i 



o dJkjdi djj~* 



tamvera." Muopeni Mulunguyu. 
Ndithudi Mulungu Ngodziwa 
zam'mitima. 

8. "E inuamene 
mwakhulupirira! Khalani 
Olungama (pokwaniritsa choona) 
cha Mulungu perekani umboni 
mwachilungamo, Ndipo kudana 
ndi anthu kusakuchititseni Kuti 
musachite chilungamo. Chitani 
Chilungamo; kutero 
kumakuyandikitsani Ku "taquwa" 
(Kuopa Mulungu). Ndipo opani 
Mulungu. Ndithudi, Mulungu 
Ngodziwa nkhani Zonse za 
(zinthu) zomwe muchita. 

9. Mulungu walonjeza omwe 
akhulupirira Ndi kuchita zabwino 
kuti adzapeza chikhululuko Ndi 
malipiro aakulu. 

10. Ndipo amene 
sadakhulupirire, Natsutsa 
zizindikiro Zathu, Iwo ndi anthu 
akumoto. 1 

11. "E! inu amene 
mwakhulupirira! Kumbukirani 
Mtendere wa Mulungu omwe uli 
painu. (Kumbukirani) pamene 
anthu ena Adatsimikiza 
kukutambasulirani manja awo 






©( 






1 Mulungu akukumbutsa Asilamu zachifundo chake powachotsera masautso 
amene anangotsala pang'ono kuwagwera ndi kuti apitirize kuyamika Mulungu 
ndi kuyadzamira kwa lye osati kumizimu ya anthu akufa, zithumwa, nyanga 
ndi mitsiriko yamtundu uliwonse. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



232 



n ftjA-i 



dJJlit 



°J>* 



(Pofuna kuchita nanu nkhondo) 
Koma adawatsekereza Manja awo 
kukufikani inu. Choncho Opani 
Mulungu. Ndipo kwa Mulungu 
Yekha, ayadzamire okhulupirira. 

12. Ndipo ndithudi, Mulungu 
adamanga pangano Ndi ana a 
Israeli, ndipo tidawaikira 
Akuluakulu khumi ndi awiri mwa 
iwo. Ndipo Mulungu adati: 
"Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi 
Inu ngati mupemphera swala 
ndikupereka Chopereka, 
ndikukhulupirira atumiki Anga, 
Ndi kuwalemekeza ndi 
kumkongoza Mulungu Ngongole 
yabwino, ndithudi 
ndikufafanizirani Zoipa zanu, 
ndikudzakulowetsani M'minda 
yomwe pansi ndi patsogolo pake 
Pakuyenda mitsinje. Koma amene 
akane Mwainu pambuyo pa 
(chipangano) Ichi, ndithu, wataika 
(kuchokera) Kunjira yowongoka". 

13. Choncho chifukwa 
chakuswa pangano lawo, 
Tidawatemberera; ndipo 
tidaumitsa mitima Yawo. 
Ankasintha mawu (a Mulungu 
Omwe adali M'mabuku a Taurat 
ndi Injili) kuwachotsa M'malo 
mwake ndipo adasiya 
Kukwaniritsa gawo lalikulu La 
zomwe adakumbutsidwa. Ukhala 



©(£)J**J&\ 



W^'S i9l* \'&< ' * 9 9 9K. * <' ' 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



233 



n tj*r\ 



O dJjlil Ojj~> 



ukuona (Iwe Mtumiki {SAW}) 
chinyengo mwa ambiri Aiwo, 
kupatula ochepa aiwo. Choncho 
Akhululukire ndi kuwaleka. 
Ndithudi, Mulungu amakonda 
ochita zabwino. 1 

14. Naonso aja amene akuti: 
"Ife ndife Akhrisitu", Tidalandira 
pangano lawo koma adasiya Gawo 
lalikulu lazomwe 
adakumbutsidwa. Tero tidaika 
pakati pawo chidani Ndi 
kusakondana mpaka tsiku 
Lomaliza. Ndipo Mulungu 
Adzawawuza zimene adali kuchita. 2 

15. " E inu anthu a Buku! 
Ndithudi wakufikani Mtumiki 
Wathu yemwe Akukufotokozerani 






1 Ndime iyi ikupitirizanso kutchula zina mwazoipa za Ayuda. Ndipo zina 
mwaizozi ndiko kusintha mawu a M'buku lawo lomwe Mulungu 
adawavumbulutsira. Iwo ankachotsamo mawu omwe sadali kuwafuna 
naikamo amene ankawafuna. 

Zoterezi Akhristu anazichitanso. Ndipo akuchitabe mpaka lero. Mabaibulo 
awo omwe akusindikiza nkuwagawa m'maiko athu kuno ku Africa ndi kwina 
kulikonse ngati utaona mofatsa lomwe asindikiza posachedwapa upeza 
kusiyana pang'ono ndi lomwe adasindikiza m'mbuyomu. (a) Mwina 
akuchotsa zimene zidalimo (b) Kapena akuikamo zomwe mudalibe (c) Mwina 
matanthauzo achiganizo amawasinthiratu kusiyana ndi momwe zidalili M'buku 
lomwe adasindikiza kale. Zonsezi zikusonyeza kuti amenewa ndiwo 
machitidwe awo pofuna kukopa anthu ambiri kuchipembedzo chawo. Akaona 
kuti ichi chikopa anthu ambiri, amachiikamo nanena kuti ndi mawu a Mulungu. 
Ndipo akaona kuti malamulo awa apirikitsa anthu amawachotsa kapena 
kuwachepetsa mphamvu yake. Umo ndimomwe alili machitidwe awo. 

2 Ndime iyi ikusonyeza kupatukana komwe kuli pakati pawo kotero kuti 
mpingo wina umayesa Unzake monga wakunja. Monga mpingo wa Roman 
Catholic umaiona mipingo ina monga ya Protestant, Orthodox ndi yambiri 
ngati mipingo ya chikunja. Zonsezi nchifukwa cha kusatsatira zophunzitsa 
zenizeni za Chikhrisitu. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



234 



^ pjir\ 



O dJJlll «jJ-» 



poyera Zambiri zomwe munkabisa 
za M'buku. Koma akusiya zambiri 
(posazilongosola).Ndithudi 
kwakudzerani kuunika Kochokera 
kwa Mulungu ndi Buku Lomwe 
likufotokoza mwatchutchutchu 
(Chinthu chilichonse). 

16. Ndibukulo Mulungu 
akuwatsogolera Kunjira 
zamtendere amene akutsata 
Chiyanjano chake ndikuwatulutsa 
Mu m'dima ndi kuwaika 
M'kuunika mwa lamulo Lake, ndi 
kuwatsogolera Kunjira yoongoka. 

17. Ndithudi, amukana 
(Mulungu) amene Akunena kuti 
Mulungu ndiye Mesiya Mwana wa 
Maria. Nena: "Ndani Angathe 
kuletsa chilichonse kwa Mulungu 
ngati lye akadafuna kuononga 
Mesiya mwana wa Mariayo ndi 
mayi Wakeyo, ndi onse omwe ali 
m'dziko Lapansi? Ndipo ufumu 
wakumwamba Ndi pansi ndi 
zapakati pake ngwa Mulungu. lye 
amalenga chimene wafuna. Ndipo 
Mulungu Ngokhoza chilichonse". 1 






>h\ ti s \ ten"* ? " hJ' 



1 Mndime iyi atchula zoyankhula zawo zamachimo zoti Isa (Yesu) ndi mwana 
wa Mulungu, kapena ndi Mulungu amene, kapena ndi mmodzi mmilungu itatu. 
Ndipo akunenetsa za kufooka kwa mneneri Yesu pamaso pa Mulungu monga 
kulili kufookanso kwazolengedwa zina. 

Ndimeyi ikunenetsanso kuti Mulungu monga amalenga mkalengedwe kamene 
lye wafuna, mchosadabwitsa kwa lye kulenga Yesu popanda tate. Ndipo 
nchosadabwitsanso kwa lye kulenga Adamu popanda tate ndi mayi. Nanga 
nchotani kuti Akhrisitu azimuyesa Mneneri Yesu kuti ndi mwana wa Mulungu 
kamba koti alibe tate? Bwanji nanga Adamu naye sakumuyesa mwana wa 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



235 



n *>■» 



o dJJlil djj^ 



18. Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu 
akunena: "Ife ndife ana a Mulungu 
ndiponso Okondeka ake". Nena: 
(Iwe Mtumiki) "Nchifukwa ninji 
Mulungu amakukhaulitsani Kamba 
kamachimo anu? Koma inu ndinu 
anthu chabe mwa omwe 
Adawalenga. Amamkhululukira 
amene Wamfuna (akalapa); ndipo 
amamulanga amene Wamfuna 
(akapanda kulapa). Ufumu 
Wakumwamba ndi pansi ndi 
zapakati pake Ngwa Mulungu. 
Ndipo Kwa lye nkobwerera." 

19. E inu anthu a Buku! 
Ndithudi, Wakudzerani Mtumiki 
Wathu Yemwe akukufotokozerani 
inu, Panthawi yopanda aneneri, 
Kuti musadzanene kuti: "Sadadze 
kwa ife wonena Nkhani zabwino 
ndiwochenjeza." Choncho 
wakudzeranidi wonena Nkhani 
zabwino ndi wochenjeza. Ndipo 
Mulungu Ngokhoza chilichonse. 

20. (Ndipo kumbukirani) 
pamene Musa adauza Anthu ake: 
"Inu anthu anga. Kumbukirani 
Mtendere wa Mulungu umene uli 
painu, Adawachita ena mwa inu 
kukhala aneneri; Ndipo 
adakuchitani kukhala mafumu 
(Pambuyo poti mudali onyozeka 
M'dziko la Iguputo m'manja mwa 



•£• 















© 



Mulungu poti nayenso alibe tate ndi mayi? Ndibwino kutsata choonadi 
ngakhale choonadicho chikuchokera kwa mdani. Choonadi ndi choonadi. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 236 1 *>» 



o djjdi djj~> 



Farawo). Ndipo wakupatsani 
zomwe Sadampatsepo aliyense 
Mwazolengedwa (mwa anthu 
anzanu)." { 

21. " Inu anthu anga. Lowani 
M'dziko loyeretsedwalo Limene 
Mulungu adakulemberani, Ndipo 
musabwerere m'mbuyo kuti 
Mungasanduke otaika." 

22. (Iwo) adati: "Iwe Musa, 
ndithudi Mmenemo muli anthu 
amphamvu. Ife sitikalowamo 
kufikira Atatulukamo okha. Ngati 
Atatulukamo, pamenepo Ndipo 
tikalowa." 

23. Anthu awiri mwa amene 
ankaopa Mulungu, omwe awiriwo 
Mulungu Adawapatsa chisomo, 
adati (Kwa anzawo): "Alowereni 
pachipata (Chadzikolo). Ngati 
mukalowamo Ndithudi, inu 
mukapambana.Ndipo kwa 
Mulungu Yekha yadzamirani ngati 
inu mulidi Okhulupirira 
(Mulungu)." 

24. (Iwo) adati: "Iwe Musa, ife 
Sitikalowamo mpang'ono pom we, 
Pomwe iwo ali momwemo. 
Choncho pita iwe ndi Mbuye 



* > \ \99\^ 9 ^ 









1 Mndime iyi akukumbutsa Ayuda chisomo chachikulu chomwe Mulungu 
adawadalitsa nacho. Kuyamika zomwe Mulungu watichitira nkofunika kwabasi. 
Tisakhale ngati anzathu awa amene Mulungu adawadalitsa ndimadalitso 
osiyanasiyana koma osamthokoza, ndiponso osamkonda ndi chikondi 
chochokera pansi pamtima. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



237 



1 *>t 



e dJJLii djj**> 



Wako, ndi kumenyana nawo; Ife 
tikhala pompano." 

25. (Musa) adati: "E Mbuye 
wanga! Ndithudi, ine ndilibe 
nyonga Koma paine ndekha ndi Pa 
mbale wanga. Choncho 
Tisiyanitseni ndi anthu Awa 
opandukira chilamulo." 

26. Mulungu adati: "Choncho 
laletsedwa Dzikolo kwa iwo 
kulilowa kwa zaka Makumi anayi. 
Akhala akuyendayenda Padziko. 
Tero, usawadandaulire Anthu 
opandukira chilamulo." 

27. Ndipo awerengere nkhani 
mwachoonadi ya ana Awiri a 
Adamu, pamene adapereka 
nsembe. Ndipo idalandiridwa ya 
mmodzi wawo. Koma Yawinayo 
siidalandiridwe. (Amene nsembe 
Yake siidalandiridwe) adati (kwa 
mnzake): "Ndithudi ndikupha." 
Mnzakeyo adati; "Ndithudi, 
Mulungu amalandira nsembe ya 
Amene akuopa (Mulungu). 1 






<"* \\\ 9 <A\ "" \'< 9 ' W*\< 






lyi ndinkhani yoyamba ya munthu wopha mnzake. Ndipo amene 
adaphedwayu ndiye munthu woyamba kulawa imfa. Wopha mnzakeyo 
ataona kuti mnzake wafadi, iye adangoti kakasi, kusowa chochita naye. Tero 
adangomsenza kumsana nkumangozungilirazungulira naye, kuopa kubwera 
naye kunyumba kuti anzake angamdziwe kuti ndiye wamupha. Makolo awo 
adali Adamu ndi Mayi Hava. Mwamwayi, khwangwala adatulukira nayamba 
kumenyana ndimnzake mpaka kumupha. Kenako namkwirira m'nthaka. 
Tsono naye uja wopha mnzake adatsanzira zomwe khwangwala adachita. 
Nakumba dzenje nkukwirira mnzakeyo. N.B! Munthu ncholengedwa 
chomalizira kudza padziko. Zidamtsogolera zolengedwa zonse ndi zaka 
miyandamiyanda. 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



238 



% *>» 



d dJjlli Ojj-*» 



28. Ngati utambasula dzanja 
lako Paine kuti undiphe, ine 
sinditambasula Dzanja langa paiwe 
kuti ndikuphe. Ndithudi, ine 
ndikuopa Mulungu Mbuye 
wazolengedwa. 

29. "Ine ndikufuna kuti usenze 
machimo Anga pamodzi ndi 
machimo ako.Choncho ukakhale 
m'gulu la anthu Akumoto. Ndipo 
iyo ndiyo Mphoto ya anthu ochita 
zoipa". 

30. Choncho adakokeka ndi 
mtima wake Kupha mbale wake, 
ndipo adamuphadi. Tero adali 
wotaika. 

31. Pamenepo Mulungu 
adatumiza khwangwala Yemwe 
amafukula pansi kuti amusonyeze 
Mmene angakwiririre mtembo wa 
m'bale wake. (Wopha mnzake) 
adati: "Kalangaine! Ndalephera 
kuti ndifanane ndi khwangwala 
Uyu, kuti ndikwirire mtembo wa 
m'bale wanga". Choncho adali 
mmodzi wodzinena. 

32. Pachifukwa chazimenezo, 
tidawalamula Ana a Israeli kuti 
amene wapha munthu Popanda 
iye (wophedwayo) kupha munthu, 
Kapena popanda kuchita 
chisokonezo Padziko, ali ngati 
wapha anthu onse.Ndipo Amene 
wamuleka munthu ali ndimoyo, 












<a'J-' JA VJ>tJ'U\ *"tf* 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



239 



1 *j*-» 



O flJU'lil 



5 J>-* 



Ali ngati awapatsa moyo anthu 
onse. Ndithudi, atumiki athu 
adawadzera ndi Zisonyezo 
zoonekera. Koma ndithu ambiri 
Aiwo, pambuyo pazimenezo, 
adapitirizabe Kuononga padziko. 

33. Choncho, mphoto ya amene 
akulimbana ndi Mulungu ndi 
Mtumiki Wake (pochita zomwe 
Waletsa) ndi kudzetsa 
chionongeko padziko, Aphedwe 
kapena apachikidwe pamtanda, 
Kapena adulidwe manja awo ndi 
miyendo Yawo mosemphanitsa 
dzanja lakumanja ndi Phazi 
lakumanzere, ndipo dzanja 
lakumanzere Ndi phazi 
lakumanja); kapena apirikitsidwe 
Mdzikomo. Uku ndikuyaluka 
kwawo padziko Lapansi. Ndipo 
iwo pa tsiku lomaliza Adzalandira 
chilango chachikulu; 1 

34. Kupatula amene alapa 
Musanawagwire. Ndipo dziwani 









'J&&m£0% 



1 Apa atchula chilango chowapatsa anthu owononga, amene amafwamba 
anthu m'njira zawo. Anthu otere alandire zilango izi:- 

(a) Ngati akungopha oyenda m'njiramo popanda kuwatengera chuma chawo 
akawapha, iwo akagwidwa chiweruzo chawo nkuphedwa nawonso. 

(b) Ngati akupha ndi kulanda chuma, atagwidwa chiweruzo chawo 
nkuphedwa. Ndipo akaphedwa choncho awapachike pamtanda kwamasiku 
atatu asanawaike m'manda. Kapena choyamba awaweruze kuti apachikidwe 
ali moyo. Ndipo akatsala pang'ono kufa, awatsitse ndi kuwamaliza. 

(c) Ngati amangolanda chuma chokha popanda kupha, akagwidwa chiweruzo 
chawo onse nkuti adulidwe dzanja lakudzanjadzanja aliyense ndi phazi 
lakumanzere. Kapena dzanja lamanzere ndi phazi ladzanjadzanja 

(d) Ngati saapha ndiponso salanda chuma, koma amangovutitsa anthu ndi 
kuwaopseza, chiweruzo chawo nkuwachotsa m'dzikomo kuwapititsa kwina 
nkuwapatsa ukaidi kumeneko, kapena kuwanjata m'dziko momwemo. 



Siirat 5. AI-Ma'idah Juzu 6 



240 1 ^> 



O dJU'til djj~*» 



kuti Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri, Ngwachisoni. 

35. E inu amene 
mwakhulupirira! Muopeni 
Mulungu ndipo funafunani Njira 
zokufikitsani kwa lye. Menyani 
nkhondo pa njira yake Kuti 
mupambane. 

36. Ndithudi, aja amene 
sadakhulupirire, Akadakhala ndi 
zonse zam'dziko Ndi zina zonga 
izo kuti azipereke Monga dipo 
kuti apulumuke kuchilango Cha 
tsiku lachimaliziro (Kiyama) 
Sizikadavomerezedwa kwa iwo. 
Ndipo iwo adzapeza chilango 
Chopweteka. 

37. Adzafuna (mwanjira 
iliyonse) Kuti atuluke kumoto, 
koma Sadzatulukamo. Ndipo 
Adzakhala ndi chilango 
chamuyaya. 

38. Ndipo wakuba wamwamuna 
ndi Wakuba wamkazi, aduleni 
manja A wo; kukhala mphoto Ya 
zomwe achita. (Ichi) ndi Chilango 
chochokera kwa Mulungu; 
Mulungu; Ngwanyonga Zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 

39. Koma amene walapa 
pambuyo Pakuchita kwake zoipa, 
nkuchita Zabwino, Mulungu 
Alandira kulapa kwake. Ndithudi, 






£1 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



241 



1 *jk-\ 



o oju'di ijj** 



Mulungu Ngokhululuka Kwabasi 
Ngwachisoni. 1 

40. Kodi sukudziwa kuti 
Mulungu Ngwake ufumu 
wakumwamba Ndi pansi? 
Amamulanga yemwe Wamfuna 
(akalakwa), ndipo 
Amamukhululukira amene 
wamfuna (Akalapa). Ndipo 
Mulungu Ngokhoza chilichonse. 

41. E iwe Mtumiki! 
Asakudandaulitse amene Akuchita 
changu kukana Mulungu mwa 
omwe Akunena ndi pakamwa 
pawo chabe: "Takhulupirira", 
pomwe mitima yawo 
Siikukhulupirira. Namonso mwa 
Ayuda, alipo Amene amadza 
kudzamvera zimene ukunena Kuti 
akanene bodza. Amene akudza 
Kudzakumvera chifukwa cha 
anthu ena amene Sadadze kwa iwe 
(omwe ndi akuluakulu awo), 
Amasintha mawu (a M'buku La 
Taurat) m'malo Mwake, omwenso 
amanena, (Kuuza otsatira awo 
kuti): "Ngati mukapatsidwe (Ndi 
Muhammad {SAW}) izi 
(takuuzanizi), Kalandireni, koma 
ngati musakapatsidwe Zimenezi 
kachenjereni." Ndipo munthu 



<&£ 












1 Taona chifundo cha Mulungu! lye akulonjeza wochimwa kuti ngati asiya 
machimo ake amlandira. Tero munthu asadzione kuti waonongeka kotero kuti 
Mulungu sangamlandire. lyayi! Abwerere ndi mtima wake wonse kwa 
Mulungu ndipo Mulungu amlandira. 



Surat 5. A I- Ma' id ah Juzu 6 



242 



■\ *>» 



O dJjdt QjJ~* 



yemwe Mulungu akufuna kuti 
amuyese mayeso sungathe 
Kumpezera chilichonse kwa 
Mulungu. Iwowo Ndiomwe 
Mulungu sadafune kuyeretsa 
Mitima yawo. Apeza kuyaluka 
padziko Lapansi. Ndipo tsiku 
lomaliza adzapeza Chilango 
chachikulu. 

42. Okonda kumvetsera 
zabodza; osaopa Pakudya (zinthu) 
zoletsedwa (zaharamu). Choncho 
akakudzera aweruze pakati Pawo, 
kapena uwapatukire. Ndipo Ngati 
uwapatukira, palibe chomwe 
Angakuvutitse nacho. Ngati 
uweruza Pakati pawo weruza 
mwachilungamo. Ndithudi, 
Mulungu amakonda olungama. 

43. Kodi angakuyese muweruzi 
Chotani pomwe iwo Ali nayo 
Taurat momwe Muli chiweruzo 
cha Mulungu pambuyo 
Powaweruza akutembenuka 
(Monyoza)! Ndipo iwo sali 
okhulupilira. 

44. Ndithudi, tidaivumbulutsa 
Taurat yokhala ndi chiongoko Ndi 
kuunika; aneneri (a Mulungu) 
Omwe adagonjera Mulungu, Adali 
kulamulira nayo Ayuda, Ndiponso 
Arabbaniyuna Ndi (aphunzitsi 
amalamulo) Ahabaru (Ansembe) 
omwe Adapemphedwa kusunga 
Buku la Mulungu ndipo iwo adali 






Will, 9' f 9 "4'''''*%. \ , 9S} 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



243 1 *>» 



O OJU'lil 



•-)>*• 



mboni pa ilo Choncho (Inu 
Asilamu) musaope anthu, Koma 
opani Ine. Ndipo musasinthanitse 
Aya (ndime) zanga ndi (zinthu za) 
Mtengo wochepa. Ndipo amene 
Sakuweruza ndi chimene Mulungu 
wavumbulutsa, iwowo ndiwo 
Osakhulupirira (okana Mulungu). 

45. Ndipo m'menemo (M'buku 
la Taurat) Tidawalamula kuti: 
"Munthu aphedwe Chifukwa 
chopha mnzake, ndi kuti diso Kwa 
diso, mphuno kwa mphuno; Khutu 
kwa khutu; dzino kwa dzino, 
Ndiponso kubwezerana mabala". 
Koma Amene wakhululuka ndiye 
kuti dipo Likhala kwaiye. Ndipo 
amene saweruza Ndi chimene 
Mulungu wavumbulutsa Iwowo 
ndiwo anthu ochita zoipa. 

46. Ndipo tidatsatiza pamapazi 
a Aneneriwo, Isa (Yesu) mwana 
wa Maria Kudzatsimikizira zomwe 
zidali Patsogolo pake M'buku la 
Taurat. Ndipo tidampatsa Injili 
Yomwe m'kati mwake muli 
chiongoko Ndi kuunika; 
Ndikutsimikizira zomwe Zidali 
patsogolo pake za M'buku la 
Taurat. Ndipo ndi chiongoko Ndi 
ulaliki wabwino kwa oopa 
(Mulungu). 

47. Anthu Abuku la Injili 
alamulire Potsatira zimene 
Mulungu Adavumbulutsa 















Surat 5. AI-Ma'idah Juzu 6 



244 



n *>» 



O dJjlll 



djj^ 



mmenemo. Ndipo amene asiya 
kulamulira ndi Zomwe Mulungu 
wavumbulutsa Iwo ndiwo 
opandukira Malamulo a (Mulungu). 

48, Ndipo takuvumbulutsira 
Buku ndi choonadi, Lomwe 
likuikira umboni Mabuku omwe 
adalipo Patsogolo pake, ndi 
kuwateteza, (monga Ponena kuti: 
"Lamulo ili ndiloona; ili iyayi"). 
Choncho weruza pakati pawo 
ndizomwe Mulungu 
wavumbulutsa, ndipo usatsate 
zofuna Zawo kusiya choona 
chomwe chakufika. Ndipo 
M'badwo uliwonse mwainu 
tidaupangira shariya (Malamulo) 
ake ndi njira yake. Mulungu 
akadafuna, akadakuikani kukhala 
Mpingo umodzi (wotsata 
chilamulo chofanana). Koma 
akufuna kukuyesani pazomwe 
Wakupatsani. Choncho pikisanani 
pazinthu Zabwino. Inu nonse 
kobwerera kwanu nkwa Mulungu. 
Naye adzakuuzani (nonsenu) mu 
Zomwe mudali kusiyana; 

49. Weruza pakati pawo 
ndichimene Mulungu 
wavumbulutsa, ndipo Usatsate 
zofuna zawo, koma Chenjera nawo 
kuti angakusokoneze Posiya zina 
mwazimene Mulungu 
Wavumbulutsa kwaiwe. Ndipo 
Ngati anyozera dziwa kuti 



®(^j3uJulpA 









up*. 



ife&to&jw 



%&$J&\&M&^ 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



245 



■wjA-1 



o dJJdi 



djj- 



Mulungu Afuna kuwapatsa 
chilango cha ena Mwa machimo 
awo. Ndithudi, Anthu ambiri 
ngopandukira (Malamulo a 
Mulungu). 

50. Kodi iwo akufuna 
chiweruzo cha nthawi yaumbuli 
(chamasiku aumbuli, Chisilamu 
Chisanadze)? Kodi ndani ali 
wabwino Polamula koposa 
Mulungu? (Izi nzodziwika) kwa 
anthu Otsimikiza (kuti Mulungu 
alipo). 

51. "E inuamene 
mwakhulupirira! Ayuda ndi 
akhrisitu musawapale Ubwenzi 
(nkumawauza chinsinsi chanu). 
Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi 
atetezi Kwa wina ndi mnzake. 
Amene awapale Ubwenzi mwa 
inu, ndiye kuti iye ndi M'modzi 
wa iwo. Ndithudi, Mulungu 
Satsogolera anthu ochita zoipa. 

52. Uwaona omwe m'mitima 
mwawo muli matenda (A 
chinyengo) akuthamangira kwa 
iwo (Ayuda) Uku akuti: "Tikuopa 
lingatigwere tsoka (Ngati 
Asilamuwa atagwa m'tsoka)". 
Koma Posachedwapa Mulungu 
abweretsa lamulo Logonjetsa 
(midzi), kapena chinthu china 
Chochokera kwa Iye (monga 
kuwaulula Achinyengo zomwe 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 246 t *}*■* 



dJJlil djj^j 



akubisa m'mitima mwawo). 
Choncho adzasanduka odzinena 
Chifukwa cha zomwe adabisa 
m'mitima mwawo. 

53. Ndipo amene adakhulupirira 
nayamba Kunena (Chitaululika 
chinyengo chawocho): "Kodi awa 
siomwe adali kulumbirira Dzina la 
Mulungu m'kulumbirira kwawo 
Kwamphamvu kuti iwo ali 
Pamodzi Ndi inu?" Zochita zawo 
zaonongeka. Tero akhala otaika. 

54. "E inu amene 
mwakhulupirira! Amene Mwa inu 
asiye chipembezo chake, Ndiye 
kuti posachedwapa Mulungu 
Adzabweretsa anthu omwe 
Awakonda, nawonso amkonda; 
Odzichepetsa kwa Asilamu 
anzawo; Amphamvu kwa 
osakhulupirira; Omenyera 
nkhondo chipembezo Cha 
Mulungu, saopa kudzudzula Kwa 
odzudzula. Umenewu ndi Ubwino 
wa Mulungu; amaupereka Kwa 
amene wamfuna. Ndipo Mulungu 
ndi Mataya; Ngodziwa kwambiri. 

55. Ndithu, Mtetezi wanu ndi 
Mulungu Ndi Mtumiki wake ndi 
omwe Akhulupirira omwe 
akupemphera Swala ndi kupereka 
chopereka Uku ali odzichepetsa. 

56. Ndipo amene achite 
Mulungu Ndi Mtumiki Wake, ndi 






®?> \\ 9 l"'y.» 9 A"A 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



247 



n *>i 



O AJU'iLl 



dj^- 



omwe Akhulupirira kukhala atetezi 
ake, (Ndithu, iwo ndi achipani cha 
Mulungu). Ndithu chipani cha 
Mulungu ndicho Chopambana. 

57. E inu amene 
mwakhulupirira! Musapalane 
nawo ubwenzi omwe 
Akuchichitira chipongwe ndi 
masewera Chipembedzo chanu 
mwa omwe Apatsidwa mabuku 
patsogolo panu, Ndiponso mwa 
osakhulupirira, Ndipo opani 
Mulungu Ngati inu mulidi 
okhulupirira. 

58. Mukaitanira kokapemphera 
Swala (Mukachita azana) 
Akuichitira chipongwe ndi 
masewera; Zimenezo nchifukwa 
chakuti iwo Ndi anthu opanda 
nzeru. 

59. Nena: "E inu anthu a Buku! 
Kodi Mukuona cholakwika kwa ife 
kaamba Kakuti takhulupirira 
Mulungu ndi Zomwe 
zavumbulutsidwa kwa ife Ndi 
zomwenso zidavumbulutsidwa 
Kale? Ndithudi, ambiri mwa inu 
ndi Opandukira chilamulo cha 
Mulungu." 

60. Nena: "Kodi ndikuuzeni za 
uja amene Ali ndimalipiro oipa 
kwa Mulungu Kuposa izi? 
Ndiomwe Mulungu 
Wawatemberera ndi kuwakwiira 



<8> 



(£$£kfr$*@i 















Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



248 1 *>» 



O oJb'dt djj^ 



Ndi kuwasandutsa ena kukhala 
Anyani ndi nkhumba, ndi 
opembeza Satana. Awo ndiwo 
okhala Ndi malo oipa, ndiponso 
osokera Njira yowongoka." 

61. Ndipo (achinyengo) 
akakudzerani, Akunena: 
"Takhulupirira", pamene Alowa 
kwa inu ali osakhulupirira Ndipo 
atulukanso ali Osakhulupirira. 
Koma Mulungu Ngodziwa 
kwambiri zomwe Akhala akubisa. 

62. Uwaona ambiri aiwo 
akuthamangira Machimo ndi 
mtopola ndi kudya Zoletsedwa. 
Ndithudi, Zimene akhala 
akuchitazo Ndizoipa kwambiri. 

63. Bwanji odziwa zamalamulo 
ndi Akuluakulu achipembedzo 
sadawaletse Zoyankhula zauchimo 
ndi kudya Kwawo zinthu 
zoletsedwa? Ndithudi, zomwe 
akhala Akuchitazo ndi zoipa. 

64. Ndipo Ayuda adati: "Dzanja 
la Mulungu Lafumbatika. 
(sitikupeza chuma ngati kale). 
(Koma sichoncho); manja awo 
ndiwo afumbatika (Posachita 
zabwino ndi kuchenjerera anthu). 
Ndipo atembereredwa chifukwa 
chazomwe anena. Koma manja 
Ake (Mulungu) Ngotambasuka. 
Amapatsa mmene wafunira. 
Ndithudi, zimene 












X.' 

#2 






Surat5. Al-Ma'idah Juzu 6 



249 



1 fr>H 



o dju'di Sjj^ 



Zavumbulutsidwa kwa iwe 
kuchokera kwa Mbuye wako, 
ziwaonjezera ambiri aiwo (Ayuda) 
Kulumpha malire ndi 
kusakhulupilira. Ndipo Taika 
chidani ndi kusakondana pakati 
Pawo mpaka tsiku lachimariziro. 
Nthawi Iliyonse akayatsa moto 
wankhondo, Mulungu 
amauzimitsa. Ndipo amayetsetsa 
Kudzetsa chisokonezo padziko, 
(Koma Mulungu sawathandiza). 
Ndipo Mulungu sakonda 
owononga. 

65. Ndipo kukadakhala kuti awa 
Anthu a Buku adakhulupirira Ndi 
kumuopa Mulungu, 
Tikadawafafanizira zolakwa Zawo, 
ndi kuwalowetsa M'minda 
yamtendere. 

66. Akadakhala kuti iwo 
adaigwiritsa ntchito Taurat ndi 
Injili, ndi zomwe 
zidavumbulutsidwa Kwa iwo 
kuchokera kwa Mbuye wawo 
(monga Qurani), ndithudi 
akanadya zakumwamba ndi 
Zapansi pamyendo yawo. Mwa 
iwo alipo Amene akutsatira njira 
yabwino. Komanso Ambiri mwa 
iwo akuchita zoipa zedi. 

67. E iwe Mtumiki! fikitsa 
(kwa anthu) Zomwe 
zavumbulutsidwa kwa iwe 
Kuchokera kwa Mbuye wako. 



*<&M£W\ffi3 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



250 1 *j*-» 



O dJjlil 5jj~j 



Ngati suchita, ndiye kuti 
sudafikitse Uthenga wake. Ndipo 
Mulungu akuteteza Kwa anthu; 
(Usaope aliyense). Ndithudi, 
Mulungu Satsogolera anthu 
osakhulupirira. 

68. Nena: "E inu anthu a 
Buku! Simuli kanthu 
(Pachipembedzo chanu) mpaka 
muimirire (Kutsatira malamulo) a 
Taurat ndi Injili Ndi zomwe 
zavumbulutsidwa kwa inu 
Kuchokera kwa Mbuye wanu, 
ziwaonjezera Kulakwa ndi 
kusakhulupirira ambiri a iwo. 
Zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe 
Kuchokera kwa Mbuye wako 
Choncho usadandaulire Anthu 
osakhulupirira. 

69. Ndithudi, amene 
akhulupirira ndi Amene ali 
m'chipembedzo cha Chiyuda, ndi 
Asabii, ndi Akhrisitu, - amene 
akhulupirire Mulungu ndi tsiku 
lomaliza, (monga Momwe 
akulangizira Mtumiki 
Muhammad{SAW}) ndipo nachita 
Zabwino, - palibe mantha kwa iwo 
Ndiponso sadzadandaula. 

70. Ndithudi, tidalandira 
pangano Kwa ana a Israeli (kuti 
adzamvera Mulungu) ndipo 
tidawatumizira aneneri. Nthawi 
iliyonse akawadzera mtumiki Ndi 
chomwe mitima yawo siinkafuna, 












®i 









®&£& 



Surat 5. AI-Ma'idah Juzu 6 



251 



n pjtr\ 



dJJlil djj_- 



Adawatsutsa ena (mwa 
atumikiwo), Ndipo ena 
ankawapha kumene. 

71. Ndipo ankaganiza kuti 
sipapezeka chilango; Tero adali 
akhungu ndi agonthi. Kenako 
Mulungu adawalandira Kulapa 
kwawo (pamene Adalapa). 
Komabe ambiri a iwo adali 
Akhungu, ndi ogontha. Ndipo 
Mulungu Akuona zimene akuchita. 

72. Ndithudi am'kana Mulungu 
amene anena kuti, "Mulungu ndiye 
Yesu mwana wa Maria", Pomwe 
Mesiya adati: "Inu ana a Israeli 
Pembedzani Mulungu Yemwe ndi 
Mbuye Wanga ndiponso Mbuye 
wanu". Ndithudi, amene aphatikize 
Mulungu ndi Chinthu china, 
ndithudi Mulungu waletsa kwa iye 
kukalowa kuMunda Wamtendere, 
ndipo malo ake ndi kumoto. Ndipo 
anthu ochita zoipa Sadzakhala ndi 
athandizi. 

73. Ndithudi, am'kana Mulungu 
amene Amanena kuti " Ndithu 
Mulungu ndi mmodzi Mwa 
(milungu) itatu", pomwe palibe 
Mulungu wina koma Mulungu 
Mmodzi yekha. Ngati sasiya 
zomwe Akunenazo, ndithudi, 
mwa iwo amene Sadakhulupirire 
chiwakhudza Chilango 
chopweteka 



tf*i*4"i^"?V*. "&rt\(*> 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



252 



1 *jA-i 



OOJlil 



Oj^ 



74. Kodi salapa kwa Mulungu 
Ndi kumpempha chikhululuko? 
Komatu Mulungu Ngokhululuka 
Kwabasi, Ngwachisoni. 

75. Mesiya mwana wa Maria 
sali chilichonse Koma ndi Mtumiki 
wa Mulungu chabe. Ndithudi, 
atumiki ambiri adapita Kale 
patsogolo pake. Nayenso mayi 
wake ndi mkazi Wachoonadi, onse 
awiri adali Kudya chakudya, 
(ndipo chotsatira chake Amapita 
kokadzithandiza. Nanga ndi 
milungu yotani yopita 
Kukadzithandiza?) Taona momwe 
Tikufotokozera kwa iwo 
zizindikiro. Taonanso mmene 
akutembenuziridwa (Kusiya 
choonadi). 

76. Nena: "Kodi 
mukupembedza Chimene 
sichingakupatseni Vuto ngakhale 
chabwino, Kusiya Mulungu? 
Pomwe Mulungu ndiye 
Wakum va; Wodzi wa. " 

77. Nena: "E inu anthu a Buku! 
Musapyole malire pachipembedzo 
Chanu popanda choonadi Ndipo 
musatsatire zofuna Za anthu omwe 
adasokera kale, Nawasokeretsanso 
ambiri, Ndi kusokera kunjira 
Yowongoka (yolungama)". 

78. Adatembereredwa amene 
Sadakhulupirire mwa Ana a Israeli 



m'^jM&$S\ 









.?.*?*. ft** 









Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 6 



253 



*>' 



oJU'lll 



°J>* 



kupyolera M'lirime la Daudi Ndi 
Yesu mwana wa Maria. Zimenezo 
nchifukwa Chakuti adanyoza 
ndipo Adali opyola malire. 

79. Sadali kuletsana choipa 
Chomwe adali kuchichita. Taona 
kuipitsitsa zomwe Adali kuchita. 

80. Uwaona ambiri aiwo 
akupalana ubwenzi ndi Omwe 
sadakhulupirire Mulungu, 
(opembedza Mafano ndi cholinga 
chomenya nkhondo Chipembedzo 
cha Chisilamu). Nzoipa Kwambiri 
zomwe adadzitsogozera okha. Tero 
Mulungu adawakwiira ndipo 
M'masautso adzakhalamo muyaya. 

81. Ndipo akadamkhulupirira 
Mulungu (Moyenera) ndi 
mneneriyo (Muhammad {SAW}) 
ndi zomwe Zidavumbulutsidwa 
kwa iye Sakadawachita abwenzi. 
Koma ambiri a iwo Ngopandukira 
chilamulo cha Mulungu. 

82. Ndithudi, uwapeza amene 
ali adani Kwenikweni kwa anthu 
omwe ali Asilamu ndi Ayuda 
komanso Amushirikina 
(opembedza mafano). Ndipo 
uwapeza oyandikira ubwenzi Ndi 
Asilamu ndi awo akunena kuti: 
"Ife ndi Akhrisitu." Zimenezo 
N'chifukwa chakuti mwa iwo alipo 
Ophunzira ndi oopa Mulungu, Ndi 
chifukwanso chakuti iwo 
(Akhirisitu) sadzitukumula. 












'9.4* %<>'<» 99"i< ' ' '<, 



Surat 5. AI-Ma'idah Juzu 7 



254 V *>i 



o Sjtfiii 



hy* 



83. Ndipo akamva zomwe 
zavumbulutsidwa Kwa Mtumiki, 
uona maso awo akugwetsa Misozi 
chifukwa cha choonadi chomwe 
Achizindikira. Akunena: "Mbuye 
wathu! Takhulupirira; choncho 
tilembeni Pamodzi ndi oikira 
umboni (choonadi)." 

84. (Atadzudzulidwa polowa 
m'Chisilamu Iwo adati): 
"Chifukwa ninji Tisamkhulupirire 
Mulungu ndi Choonadi chatifika, 
pomwe Tikuyembekezera Mbuye 
wathu Kukatilowetsa (kumunda 
wamtendere) Pamodzi ndi anthu 
abwino?" 

85. Choncho Mulungu 
Adzawalipira, pazomwe Adanena, 
minda yomwe Pansi ndi patsogolo 
pake Mitsinje ikuyenda. 
M'menemo Adzakhala muyaya. 
Imeneyo ndiyo mphoto Ya ochita 
zabwino. 

86. Ndipo amene 
sadakhulipirire, Nkutsutsa 
zizindikiro Zathu, iwowo ndiwo 
Anthu akumoto. 

87. E inu amene 
mwakhulupirira! Musazichite 
zabwino zomwe Mulungu 
wakulolezani kukhala Zoletsedwa. 
Ndipo musalumphe Malire, 
ndithudi Mulungu Sakonda anthu 
olumpha malire. 















®r. 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



255 V ,>» 



OJU'lil 



°J>- 



88. Idyani zabwino zomwe 
Mulungu Wakupatsani zomwe zili 
zololedwa. Ndipo opani Mulungu 
yemwe inu Mukumkhulupirira. 

89. Mulungu sangakulangeni 
chifukwa Chakulumbira kwanu 
kopanda pake. Koma akulangani 
kamba ka Malumbiro omwe 
mwalumbira Motsimikiza. 
Choncho dipo lake Ndikuwadyetsa 
osauka khumi ndi Chakudya cha 
mlingo wapakatikati Chomwe 
mumawadyetsa anthu Anu; kapena 
kuwaveka, kapena Kumpatsa ufulu 
kapolo. Koma Amene sangapeze 
zimenezo, asale Masiku atatu. Hi 
ndi dipo Lakulumbira kwanu 
pamene Mukulumbira. Ndipo 
sungani Malumbilo anu, (musaswe 
chomwe Mudalumbirira). Motero 
ndi Momwe Mulungu 
akukufotokozerani Zizindikiro 
Zake kuti muthokoze. 

90. E inu amene 
mwakhulupirira! Ndithudi, mowa 
(kutchova) njuga, Kupembedza 
mafano ndi kuombeza Maula, 
(zonsezi) ndi uve, Mwa ntchito za 
Satana. Choncho Zipeweni kuti 
mupambane. 

91. Ndithudi, Satana akufuna 
kudzetsa Chidani ndi kusakondana 
pakati Panu kudzera m'mowa ndi 
Njuga, ndikuti akutsekerezeni 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 I 256 I V *> 



o dJjlil ojj^ 



Kukumbukira Mulungu Ndi 
kupemphera Swala. Kodi inu 
simusiya? 

92. Mverani Mulungu, ndipo 
mverani Mtumiki wake ndipo 
chenjerani (Musanyoze malamulo 
a Mulungu). Ngati munyoza, 
dziwani kuti udindo wa Mtumiki 
wathu ndikufikitsa uthenga 
Woonekera basi. (Ngati atafikitsa 
Uthenga, palibe kudzudzulidwa iye) 

93. Palibe tchimo kwa amene 
akhulupirira Ndikuchita zabwino 
pazomwe Adadya 
(zisadaletsedwe) Ngati akupitiriza 
kuopa ndikukhulupirira Ndikuchita 
zabwino; kenako nkuopanso 
(Ataletsedwa zina) 
ndikukhulupirira; (Atalamulidwa 
zinanso) nkuopanso Ndikuchita 
zabwino. Ndipo Mulungu, 
amakonda ochita zabwino. 

94. E inu amene 
mwakhulupirira! Ndithu Mulungu 
Akuyesani ndi nyama zina 
zozichita ulenje, zomwe Manja 
anu ndi mikondo yanu ingazifikire, 
kuti Mulungu amuwonetsere 
poyera amene akumuopa 
Mwanseri. Ndipo amene alumphe 
malire (posaka Nyamayo ndi 
kupha) pambuyo pazomwe 
Mwauzidwazo, adzapeza chilango 
chopweteka. 












Surat 5. Ai-Ma'idah Juzu 7 



257 



V *j*-» 



aJU'lil Ojj~t 



95. E inu amene 
mwakhulupirira! Musaphe nyama 
Yamtchire pomwe inu muli 
m'mapemphero a Haji Kapena 
Umura. Ndipo amene angaphe 
mwadala Nyama ya mtchireyo 
mwa inu, dipo (lake likhale 
Kuzinga) yofanana ndi yomwe 
waphayo, mumtundu Wanyama 
zowetedwa, (monga mmene) 
angaweruzire Olungama awiri a 
mwainu. Nyama yansembeyo 
Iperekedwe ku Ka'aba (kuti 
ikazingidwe kumeneko 
Ndikuwagawira osauka); kapena 
alipe dipo Lachakudya kudyetsa 
masikini; kapena m'malo Mwake 
asale kuti alawe kupweteka kwa 
chinthu Chakecho. Ndipo Mulungu 
afafaniza zomwe zidapita Kale. 
Koma amene achitenso, Mulungu 
amukhaulitsa Ndi chilango 
chochokera kwa lye. Ndipo 
Mulungu Ngwamphamvu zoposa, 
Wokhaulitsa koopsa 

96. Nkololezedwa kwa inu 
kusaka nyama Zam'nyanja ndi 
chakudya chake (chomwe 
Chapezeka m'nyanjamo chitafa 
chokha). Chimenecho ndi kamba 
wanu (Inu amene simuli paulendo) 
ndiponso Apaulendo. 
Kwaletsedwa Kwa inu kusaka za 
pamtunda Pomwe muli 
m'mapemphero a Haji Kapena 









Siirat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



258 



V *j*-i 



OJtftil Ojj-j 



Umura. Opani Mulungu Yemwe 
kwa lye mudzasonkhanitsidwa. 

97. Mulungu wapanga Ka'aba 
kukhala nyumba Yopatulika, 
ndikukhala pamalo popezera 
zosowa Za anthu. Ndipo 
adapanganso miyezi (inayi) 
Yopatulika, ndikupereka nyama 
zansembe ku Makka zovekedwa 
makoza monga zisonyezo 
(Kusonyeza kuti zikupita ku 
Makka). Zonsezi Nkuti mudziwe 
kuti Mulungu akudziwa 
Zakumwamba ndi pansi, ndikuti 
Mulungu Ngodziwa chilichonse. 

98. Dziwani kuti ndithudi, 
Mulungu Ngolanga Mwaukali. 
Ndikutinso Mulungu Ngokhululuka 
Kwabasi, Ngwachisoni. 

99. Pamtumiki palibe china 
koma Kufikitsa chabe (uthenga). 
Ndipo Mulungu akudziwa zimene 
Mukuzionetsera poyera ndi 
Zimene mukuzibisa. 

100. Nena (kwa aliyense kuti): 
Zoipa ndi zabwino Sizingafanane 
ngakhale Kutakusangalatsa 
kuchuluka Kwa zoipazo 
(usapendekere Kuchuluka 
kwakeko); choncho Opani 
Mulungu, ee! Inu eni Nzeru kuti 
mupambane." 

101. E inu amene 
mwakhulupirira! Musamafunse za 






m&d&^wSfci 












iBJ^SESSa^® 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



259 V «jfci 



O dJjlil djj-i 



zinthu zomwe Zitasonyezedwa 
kwa inu zikuipirani. Ndipo ngati 
muzifunsa pomwe Qur'an 
ikuvumbulutsidwa, zionetsedwa 
kwa inu. Mulungu wakhululuka 
zimenezo. Mulungu Ngokhululuka 
kwabasi Ndiponso Ngoleza 

102. Anthu amene adalipo kale 
inu Musanadze, adazifunsapo 
Zotere. Ndipo pachifukwa 
chimenecho Adasanduka 
osakhulupirira. 

103. Mulungu sadaike 
(kuletsedwa Kwamtundu 
uliwonse) panyama Yotchedwa 
Bahira, ngakhale Saiba, Wasila, 
ngakhalenso Hami. Koma amene 
sadakhulupirire Akumpekera 
Mulungu bodza. Ndipo ambiri 
aiwo Sagwiritsa ntchito nzeru 
zawo. 

104. Ndipo akauzidwa: 
"Tadzani kuchilamulo Cha zomwe 
Mulungu wavumbulutsa ndi 
(zomwe Akunena) Mtumiki," 
Akunena: "Tikukwaniritsidwa ndi 
zomwe tidawapeza nazo makolo 
athu," Kodi chinkana kuti Makolo 
awowo sadali kudziwa chinthu 
Chilichonse ndipo sadali oongoka, 
(Awatsatirabe)? 

105. E inu amene 
mwakhulupirira! Chimene chili 
chofunika kwa inu ndi 






\j?^jp$& t^* f y QUoS 












><'^<&\SM$ 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



260 



V *j*-1 



DJJlil d 



dj^-* 



Kudziganizira nokha. Ndipo 
amene Asokera sangakupatseni 
mavuto Ngati inu mutalungama. 
Nonsenu Kobwerera kwanu nkwa 
Mulungu basi. Choncho 
adzakuuzani zimene mudali 
kuchita. 

106. E inu amene 
mwakhulupirira! Pamene 
chamfikira mmodzi wa inu 
Chisonyezo cha imfa, ndipo 
akufuna kusiya chilawo (Mawu 
omaliza) funani Mboni ponena 
mawuwo. Aikire umboni Awiri 
olungama mwa inu (Asilamu) 
Kapena apadera ngati muli 
paulendo, ndipo Zisonyezo zaimfa 
zitaonekera. Ngati mutazikaikira 
Zitsekerezeni (kuti zisachoke) 
mboni Ziwiri pambuyo pa Swala 
(yomwe Amasonkhana anthu 
ambiri), ndipo Zilumbirire m'dzina 
la Mulungu kunena (Kuti): 
"Sitikusinthanitsa Malumbirowa 
ndi china chake ngakhale 
Chitakhala chothandiza kwa ife 
Kapena mmodzi mwa abale athu. 
Sitikubisa umboni umene Mulungu 
Watilamula kuti tiupereke moona. 
Ife ngati titabisa umboni (kapena 
Kuyankhula chonama), ndithudi 
tikhala Mwa anthu ochimwa." 

107. Koma ngati kutaoneka kuti 
mboni Ziwiri zija zanama pa 
umboni wawo, Kapena zabisa 












Surat 5. AI-Ma'idah Juzu 7 



261 



V*>l 



O Sjtflll 



aj^ 



chinthu, apo awiri Achibale a 
wakufayo aimirire m'malo Mwa 
mboni ziwirizo, (pambuyo paswala 
Kuti aulule zabodza lawo). 
Choncho Alumbirire m'dzina la 
Mulungu kuti: "Ndithu kulumbira 
kwathu nkoyenera 
Kuvomerezedwa kuposa 
Kulumbira kwawo; ndipo 
sitinapyole malire (Mukulumbira 
kwathu). Ndipo sitikuzipekera 
Mbonizo bodza. Ndithudi, ngati ife 
Titachita zotere, ndiye kuti tikhala 
Mwa ochita zoipa, (oyenera 
kulandira Chilango cha 
Mulungu)." 

108. Chilamulochi ndi njira 
yapafupi kuti Mboni zikwaniritse 
umboni wawo mnjira Yoyenera, 
(ndikuti zisamalire Kulumbira 
Mulungu kwawo); kapena kuopa 
Kuyaluka bodza lawo likaonekera 
Poyera, pambuyo polumbira 
enawo (Izi zili polumbira amlowa 
mmalo pokana Umboni wawo). 
Ndipo opani Mulungu 
(mkulumbira kwanu Ndi 
kukhulupirika kwanu) ndipo 
Mverani malamulo Ake. Mulungu 
Satsogolera anthu opandukira 
chilamulo Chake. 

109. (Kumbukirani) tsiku 
lomwe Mulungu Adzasonkhanitsa, 
aneneri Ndikuwafunsa kuti: "Kodi 
Mudayankhidwa chiyani?" 









X3\ 






Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



262 V *>i 



OJU'lil 



Oj^ 



Aneneri adzati: "Ife sitidziwa 
Ndithudi, inuyo Ndiye Wodziwa 
zamseri." 

110. Kumbukiraninso pamenne 
Mulungu adzati: "Iwe Yesu 
mwana wa Mariya! Kumbuka 
chisomo Changa pa iwe ndi pa 
mayi wako, pamene 
Ndinakuthandiza ndi mzimu 
woyera (Gabriel) Kotero kuti 
udalankhula kwa anthu (mawu 
Omveka) pamene udali mchikuta 
ndiponso Pamene udali wamkulu. 
Ndipo (kumbuka) pamene 
Ndidakuphunzitsa kulemba , 
nzeru; (Ndinakuzindikiritsanso 
Buku la) Taurat ndi Injili. 
(Kumbukanso) pamene udaumba 
dongo chithunzi Chambalame 
mwalamulo langa. Utatero 
udauziramo Ndipo zidasanduka 
mbalame mwalamulo langa. 
Ndipamene udali kuchiza akhungu 
ndi akhate, Mwalamulo langa. 
Ndipamene unkawatulutsa 
(M'manda) enamwaakufa 
mwalamulo langa. Ndipamene 
ndinawatsekereza ana a Israeli kwa 
iwe (Kuti asakuzunze) pamene 
udawadzera ndi Zisonyezo 
zooneka, ndipo aja mwaiwo omwe 
Sadakhulupirire, adati: Ichi 
sichina, koma ndi Matsenga 
owonekera. 

111. Ndipo (kumbukira) 
pamene Ndidawaululira ophunzira 






b&\$(&9\&&M$ 



Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



263 



V*>l 



o *JJ\L\ i 



9jf* 



ako Kuti: "Ndikhulupirireni Ine 
ndi Mtumiki wanga (uyu Yesu)." 
Iwo adati: "Takhulupirira; ndipo 
Khalani mboni kuti ife ndife 
Ogonjera (tadzipereka mwa Inu)." 

112. (Kumbukira) pamene 
ophunzira ako adati : "I we, Yesu 
mwana wa Mariya: Kodi Mbuye 
Wako angathe kutitsitsira 
chakudya kuchokera 
Kumwamba?" (Yesu) adati: 
"Opani Mulungu, ngati Inu mulidi 
okhulupirira. (Musamangopempha 
Zozizwitsa)." 

113. (Iwo) adati: "Tikufuna 
kudya Chimenecho, ndikuti mitima 
yathu Ikhazikike, Ndikutinso 
tidziwe Kuti watiuza choona; tero 
kuti Tikhale oikira umboni 
pachimenecho." 

114. Yesu mwana wa Mariya 
adati: "Inu, Mulungu Mbuye 
wathu! Titsitsireni chakudya 
kuchokera Kumwamba kuti 
chikhale Chikondwerero cha 
oyambirira Ndi omaliza mwa ife, 
komanso Chikhale chisonyezo 
chochokera Kwa inu; choncho 
tipatseni Ndithu, inu ndinu abwino 
Popatsa kuposa opatsa." 

115. Mulungu adati: "Ndithu, 
Ine Ndikuchitsitsa kwa inu. Koma 
amene adzatsutse Mwa inu 
pambuyo pa ichi, Ndithu, Ine 



KV»^8K&%; 



*?K 99 



®(z&z 



*\l<f ft < J '?*\Z.»"\ ' 









Siirat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 



264 



V *>» 



o Sju'lil Ijj^t 



ndidzamulanga Ndi chilango 
chomwe Sindidamulangepo nacho 
Aliyense mwazolengedwa." 

116. Ndipo (kumbukirani) 
pamene Mulungu adzanena: "Iwe 
Yesu mwana wa Mariya: Kodi iwe 
udauza Anthu kuti," "Ndiyeseni 
ine Ndi mayi wanga monga 
Milungu iwiri m'malo mwa 
Mulungu?" (Mneneri Yesu) 
adzaati: "Ulemerero ukhale pa Inu. 
Sikoyenera Kwa ine kunena 
zomwe sizili Zoyenera (kwa ine 
mawu amenewa Ngabodza). Ngati 
ndikadanena, Ndiye kuti 
mukadadziwa. Inu Mukudziwa 
zomwe zili mumtima Mwanga, 
pomwe ine sindidziwa Zomwe zili 
mwa inu. Ndithudi, Inu ndinu 
Wodziwa zamseri, 

117. Sindinawuze chilichonse 
kupatula Chimene mudandilamula 
kuti; "Pembedzani Mulungu, 
Mbuye wanga Ndiponso Mbuye 
wanu". Ndipo ndinali Mboni kwa 
iwo pamene ndidali nawo. Koma 
pamene mudanditenga, Inu ndiye 
Mudali muyang'aniri paiwo; ndipo 
Inu ndinu Mboni yachilichonse. 

118. "Ngati muwalanga, 
ndithudi Iwo ndi akapolo anu. 
Ndipo mukawakhululukira, 
Ndithudi, inu ndinu Mwini 
Mphamvu zoposa, Wanzeru 
zakuya." 



©y\yJ*S(^J 












Surat 5. Al-Ma'idah Juzu 7 265 V *>i 



OJJlil OjJ~" 



119. Mulungu adzati: "Hi ndi 
tsiku lomwe olankhula zoona 
Kudzawathandiza kuona Kwawo. 
Iwo adzalandira Minda yomwe 
pansi ndi Patsogolo pake mitsinje 
Ikuyenda. M'menemo Adzakhala 
muyaya. Mulungu adzawayanja; 
Naonso adzayanja zomwe 
Adzapatsidwa ndi Mulungu. 
Kumeneko ndiko kupambana 
Kwakukulu. 

120. Mulungu yekha ndiye 
mwini ufumu Wakumwamba ndi 
pansi, ndi Zam'menemo. lye 
Ngokhoza Chilichonse. 






*«? »'*" •» 



S^VtfUPCW^ 







Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



266 



V*>i 



1 fUi*i|1 5jj-*» 




SURAT AL-AN'AM VI 




Surayi yalangiza anthu kuti alingalire dziko ndizammenemo, 
zomwe zikusonyeza ukulu wa Muyambitsi; Mulungu 
wolemekezeka. Ndi kuti palibe womthandiza mkulenga. 
Ndiponso sathandizana ndi aliyense polandira mapemphero. 
Ndiponso salingana ndi aliyense mwazolengedwa Zake. 
M' surayi muli nkhani za ena mwa aneneri. Ndipo yayamba 
kusimba nkhani ya Ibrahim (A.S.) Ndipo yanenetsa kuti iye 
adamdziwa Mulungu kupyolera mkumpenyetsetsa molingalira 
za chilengedwe cha zakumwamba monga nyenyezi, dzuwa ndi 
mwezi. 

Surayi ikuphanula maso a anthu kuti ayang'ane zinthu 
momwe zikuchitikira; momwe chamoyo chimatulukira m'chakufa. 
Ndipo yafotokozanso makhalidwe a anthu amakani, otsutsa kuti 
amangokangamira maganizo okhala kutali ndi choonadi. 

M'surayi mwafotokozedwanso zinthu zahalali ndi zaharamu. 
Ndi kuti udindo wopanga chinthu kukhala chahalali kapena 
haramu ngwa Mulungu. Ndipo m' Surayi mulinso malamulo 
oletsa kupembedza mafano, kuchita chiwerewere, kupha anthu, 
kudya chuma cha masiye, ndi kuti miyeso ndi masikero 
ziyesedwe modzazitsa, kukwaniritsa chilungamo pamachitidwe 
onse, kusunga chipangano ndi kuchitira zabwino makolo. 




Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



267 



V*>l 



n fUoVi Sjj-- 



Surat Al-An'am VI 



M^mmz'' 



m 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuyamikidwa konse 
kwabwino nkwa Mulungu, Yemwe 
adalenga thambo ndi Nthaka, 
napanga mdima ndi kuunika, 
Pamwamba pa izi, amene 
sadakhulupirire Mbuye wawo 
akumfanizira Mulungu ndi 
Milungu yabodza. 

2. lye ndi Yemwe adakulengani 
ndi Dongo, ndipo kenako adaika 
nthawi (Yothera cholengedwa 
chilichonse), Ndi nthawi ina 
yodziwika kwa lye (Yomwe 
njoukitsira zolengedwa ku imfa). 
Ndipo pa izi inu (osakhulupirira) 
Mukukaikira. 

3. Ndipo lye ndi Mulungu 
(Wopembedzedwa) Kumwamba 
ndi pansi. Akudziwa za Mkati 
mwanu ndi zakunja kwanu, Ndipo 
akudziwa zimene mukupeza 
(Kuchokera mzochitachita zanu, 
Zabwino kapena zoipa). 

4. Ndipo palibe pamene 
Chikuwadzera chisonyezo 
Chilichonse mwa zisonyezo Za 
Mbuye wawo koma 
Akuzitembenukira kumbali. 



Q&i&^Wj 



-^ 






©< 



x& 






'\S-"J 9 \ 1*9%*?' ^'^'i 









" 9 • 99X'>' 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



268 



V *>l 



% fUiSH fljj-» 



5. Ndithudi, atsutsa choonadi 
(Qur'an) parnene Chawadzera. 
Posachedwapa ziwafika Nkhani 
(za zilango) zimene adali 
Kuzichitira chipongwe. 

6. Kodi saona kuti ndi mibadwo 
ingati Tidaiononga patsogolo 
pawo? Tidawapatsa mphamvu 
yopezera za M'dziko zomwe 
sitidakupatseni inu Ndipo 
tidawavumbwitsira mvula 
Yopitiriza (mwaubwino choncho, 
Adasangalala kopambana). Ndipo 
Tidaipanga mitsinje kuyenda pansi 
Pawo (pansi pa mitengo yawo ndi 
Nyumba zawo). Kenako 
tidawaononga Chifukwa cha 
machimo awo, ndipo Pambuyo 
pawo tidalenga mibadwo ina. 

7. Ndipo ngati tikadakutsitsira 
Malemba (olembedwa) 
m'mapepala, (Monga momwe 
adakufunsira), nkuwakhudza Ndi 
manja awo, amene Sadakhulupirire 
akadati: "Ichi sichina koma ndi 
matsenga owoneka." 

8. Ndipo amanena: "Bwanji iye 
Osamtsitsira Mngelo (kuti Aziikira 
umboni kwa anthu za Uneneri 
wake)?" Tikadakutsitsira Mngelo 
(nkusakhulupirira), Ndithu, 
chiweruzo chakuonongeka Kwawo 
chikadakwaniritsidwa. Ndipo 
Sakadapatsidwanso mpata. 















Siirat 6. AI-An'am Juzu 7 



269 V *>i 



*\ {\*iH\ 5jj-» 



9. Ndipo tikadampanga Mngelo 
kukhala M'tumiki, 
tikadamsandutsa kukhala Munthu 
(chifukwa iwo sangathe Kumuona 
Mngelo), ndipo tikadati 
Asakanikirane nawo monga 
Momwe eni amasakanikirana 
(kotero Kuti sakadamdziwa kuti 
Mngelo ndi uyu). 

lO.Ndithudi, adachitidwa 
chipongwe Atumiki patsogolo 
pako; koma (Mapeto ake) aja mwa 
iwo omwe Adachita chipongwe 
zidawazinga Zomwe adali 
kuzichitira chipongwe. 

ll.Nena: "Yendani pa dziko, 
kenako tayang'anani momwe 
adalili mapeto Aotsutsa." 1 

12. Nena (mowafunsa): 
"Nzayani zomwe Zili kumwamba 
ndi pansi?" Nena Kwa iwo (ngati 
sakuyankha): "Nza Mulungu". lye 
wadzikakamiza Kuwachitira 
chifundo (anthu Ake). 
(Pachifukwa chimenechi 
amawapatsa Nthawi osawalanga 
mwachangu). Ndithudi 
adzakusonkhanitsani Tsiku la 
Kiyama lopanda chikaiko. Amene 
Adzitaya okha, sakhulupirira (Za 
tsikulo). 



* 9 J %' fX » <■* 









1 Apa tanthauzo nkuti tayendani padziko mukayang'ane ndi kulingalira zilango 
zopweteka zimene zldawatsikira anthu akale. Kuyang'ana ndi kulingalira 
zoterezo kuti zikhale phunziro kwa inu kuti musachitenso zimene 
zidawagwetsa kuchionongeko. 



Siirat 6. Al-An'am Juzu 7 



270 



V *>i 



*\ ^ usSh 5jj~> 






13.Nza lye (Mulungu) Zonse 
zili munthawi Ya usiku ndi usana. 
lye Ngwakumva, Ngodziwa." 

14.Nena: "Ndidzipangire 
mtetezi Wanga kusiya Mulungu, 
Mlengi Wathambo ndi nthaka? lye 
Njemwe Amadyetsa ndipo 
sadyetsedwa." Nena: 
"Ndalamulidwa kukhala Woyamba 
mwa olowa M'chisilamu," Ndipo 
(ndauzidwa kuti): "Usakhale mwa 
ophatikiza (Mulungu Ndi 
mafano)" 

15. Nena (kwa iwo): "Ine 
ndikuopa chilango Cha tsiku 
lalikulu Ngati ndinyoza Mbuye 
wanga." 

16. Yemwe adzapewetsedwe 
(Chilangocho) tsiku limenelo, 
Ndiye kuti wamchitira chifundo; 
Kumeneko nkupambana 
kowonekera. 

17. "Ngati Mulungu 
atakukhudza ndi Mazunzo, palibe 
aliyense angathe Kukuchotsera, 
koma lye basi; ndipo Ngati 
atakukhudza ndi zabwino (palibe 
Amene angakutsekereze ku 
Zabwinozo). lye ali ndi mphamvu 
paChilichonse. 1 



1 Mu aya iyi Chauta akuuza Mtumiki Wake ndi omtsatira ake kuti ngati 
masautso atampeza umphawi ndi matenda, palibe amene angamchotsere 
zimenezi koma Mulungu basi. Ndiponso ngati zitamkhudza zabwino, monga 
kukhala ndi moyo wangwiro ndi chuma chambiri, palibe amene angazichotse 
zimenezi kwa iye ngati Mulungu safuna. Choncho tiyeni tiike chikhulupiriro 
chathu chonse mwa Mulungu. 






*±l' '*Z<* *9*99* 9 S919* 



Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



271 I V *>» 



*\ f UiSfi 3jj-» 



18. lye ndi Mgonjetsi pa anthu 
ake (Onse); lye Ngwanzeru 
zakuya, Wodziwa nkhani zonse. 

19.Nena: "Kodi nchinthu chanji 
chomwe Umboni wake uli 
waukulu koposa?"Nena (ngati 
sakuyankha) : "Ndi (umboni Wa) 
Mulungu basi. (lye) ndi mboni 
Pakati pa ine ndi inu. Ndipo 
Qur'an iyi yavumbulutsidwa kwa 
ine Kuti ndikuchenjezeni nayo ndi 
amene Yawafika (pali ponse 
pamene ali). Kodi inu 
mukutsimikiza ndi kuikira Umboni 
kuti pali milungu ina Pamodzi ndi 
Mulungu?" Nenanso: "Koma ine 
sindikuikira umboni." Nenanso: 
"lye ndi Mulungu mmodzi Yekha. 
Ndithudi, ine ndili kutali ndi 
zomwe mukumphatikiza nazo." 

20. Omwe tidawapatsa Buku 
akumzindikira 

(Muhammad{SAW} bwinobwino) 
monga Momwe akuwazindikirira 
ana awo. Koma omwe adziononga 
okha, iwo Sangakhulupirire. 

21. Kodi ndani woipitsitsa zedi 
Woposa yemwe akum'pekera 
Mulungu bodza. Kapena kutsutsa 
Zizindikiro zake? Ndithudi, oipa 
sangapambane. 

22. Ndipo (akumbutse) tsiku 
lomwe Tidzawasonkhanitsa onse 
pamodzi ;Kenako tidzati kwa 















Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



272 V *>i 



*\ pUity 5jj~* 



omwe adali Kuphatikiza (Mulungu 
ndi mafano): "Ali kuti aphatikizi 
anu aja omwe Munkati 
ngothandizana ndi Mulungu?" 

23. Ndipo dandaulo lawo 
silidzakhala Lina koma kunena: 
"Wallahi,Tikulumbirira Mulungu 
Mbuye Wathu, sitidali ophatikiza 
mafano Ndi Mulungu." (Uku 
kudzakhala Kuyesera kumunamiza 
Mulungu). 

24. Taona momwe 
akudzinamizira okha Ndipo 
zidzawataika zomwe adali Kuzipeka 
(ponena kuti izo ndi Milungu 
zidzawapulumutsa Kwa Mulungu). 

25. Alipo ena mwa iwo omwe 
akukumvetsera (Ukamawerenga 
Qur'an) ndipo taika Zitsekero 
pamitima yawo kuti Asazindikire 
(chifukwa cha machimo Awo 
omwe akhala akuchita). Ndi 
M'makutu mwawo kulemera kwa 
ugonthi;Ndipo akaona chozizwitsa 
chilichonse,Sakuchikhulupirira,Ku 
fikira akakudzera kudzakangana 
nawe.Awo amene sadakhulupirire 
akuti:"Izi (zimene utilankhulazi), 
Sikanthu koma ndi nkhani zopeka 
Za anthu akale." 

26. Ndipo iwo akuletsa (anthu 
kutsatira) izi, Ndipo (eniwo) 
akudziika nazo kutali. Palibe Wina 
akumuononga koma iwo okha, 
asakudziwa. 















9 V*i 9 C 'K 9 *" K>' *9'\'*?' 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



273 



V*>i 



% f toty *jj~* 



27. Ndipo ukadaona (tsiku la 
Kiyama) Pamene adzawaimitsa 
pamoto Nkuyamba kunena: "Ha! 
Tikadabwezedwa (kudziko 
lapansi) Ndipo sitikadatsutsanso 
zizindikiro Za Mbuye wathu; 
tikadakhala mwa Okhulupirira" 
(Ukadaona tsikulo M'mene 
azikasinkhirasinkhira Atathedwa 
nzeru). 

28. (Sichoncho sadzachita 
chilichonse Chabwino.) Koma 
zawaonekera poyera Zomwe adali 
kubisa kale. Ndipo 
Akadabwezedwa akadabwerezanso 
Kuchita zimene adaletsedwa. 
Ndithudi Iwo ngabodza basi. 

29. Akumanena: "Palibe china 
koma Moyo wathu wapadziko 
lapansi basi. Ndipo ife 
sitidzaukitsidwanso M'manda". 

30. Ndipo ukadaona (tsiku la 
chiweruzo) Pamene 
azikaimitsidwa pamaso pa Mbuye 
wawo nauzidwa: "Kodi ichi 
Sichoona?" (Iwo) nati: "Inde 
Nchoona: tikulumbira Mbuye 
Wathu." (Mulungu) adzati: 
"Lawani chilango chifiikwa Cha 
kusakhulupirira kwanu kuja 
(Aneneri a Mulungu)." 

31. Ndithudi, ataika ndi 
kuonongeka Amene akutsutsa 
zokumana ndi Mulungu, mpaka 






iV- » "»■*».! v^t2t<s »>1i-"' V 









Surat 6. AI-An'am Juzu 7 I 274 1 V *j*-» 



1 f\juH\ 5jj-» 



mwadzidzidzi nthawi Ya kiyama 
itawafikira ndipo nati: "Ho! 
Masautso paife chifukwa 
chakusalabadira kwathu kuja." 
Uku iwoAtasenza mitolo 
yamachimo kumisana Kwao. 
Taonani kuipa kwa zomwe 
akusenza. 

32. Ndipo moyo wadziko lino 
lapansi Sikanthu, koma ndi 
masewera (chibwana). Ndiponso 
chabe. Koma nyumba Yomaliza 
ndi yabwino koposa,(Siyofanana 
ndi chisangalalo Chapadziko 
lapansi) kwa omwe Akuopa 
Mulungu. Bwanji simuzindikira? 

33. Ndithu, tikudziwa kuti 
zikukudandaulitsa zomwe 
akukunenera (Pokunyoza ndi 
kukuyesa wabodza).Iwo sakutsutsa 
iwe; koma oipawa Akutsutsa 
zizindikiro za Mulungu. 

34. Ndithudi, Aneneri onse 
adatsutsidwa Iwe usadadze. Koma 
adapirira Kuzomwe adatsutsidwa, 
ndipo Adazunzidwa kufikira 
pamene Chipulumutso chathu 
chidawafika. Palibe wosintha 
mawu a Mulungu (Malonjezo a 
Mulungu). Ndithu, Zakufika 
nkhani za Atumiki (Momwe muli 
malingaliro ndi Maphunziro 
ambiri). 

35. Ndipo ngati nkovuta kwa 
iwe kudzipatula Kwawoku (ndi 












>> JLf It ' \ 9X9 \'\ 9 V\$ K' 



$$&$&&&& 



Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



275 



V*>i 



*\ pUity 5jj-> 



zomwe wadza nazozi Pomwe iwo 
akukuumiriza kuti uwabweretsere 
Chozizwitsa, nawe Nkumafuna; 
zikadatero, pomwe Ine 
Sindikufuna); choncho, ngati uli 
Wokhoza kufunafuna njira yapansi 
Penipeni m'nthaka (kukafuna 
Zozizwitsazo), kapena (ungathe 
Kupeza) makwerero nkukwera 
kumwamba nkubwera ndi 
chozizwitsa (Chimene akufuna, 
chita). Mulungu Akadafuna 
akadawasonkhanitsa onse 
Kuchiwongoko. Choncho, 
usakhale Mwa osazindikira zinthu. 

36. Ndithudi amene 
akuvomereza, ngomwe akumva. 
(Ndipo anthu awa amene safuna 
Kumvera chilichonse ndi akufa 
Ngakhale ali moyo). Ndipo akufa 
Mulungu Adzawaukitsa (m'manda 
mwawo) kenako Adzabwezedwa 
kwa lye. 

37. Ndipo (iwo) akumanena: 
"Bwanji Sichinatsitsidwe 
chozizwitsa kwa iye Kuchokera 
kwa Mbuye wake?" Nena: 
"Ndithudi, Mulungu Ngokhoza 
kutsitsa Chozizwitsa koma ambiri 
aiwo sadziwa (Zomwe Mulungu 
afuna)." 

38. Ndipo palibe nyama ili 
yonse M'nthaka, ngakhale 
mbalame yowuluka Ndi mapiko 
ake awiri koma ndi magulu 



<j££ll L$& JJ&5 $<£&1\ 












Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



276 



V *>l 



n pUity djj-j 



Azolengedwa ngati inu (Zomwe 
Mulungu adazilenga). Sitinasiye 
chinthu chilichonse Kapena 
kuchinyozera chilichonse M'Buku 
(chomwe nchofunika Koma 
tachifotokoza).Ndipo tero 
adzawasonkhanitsa Kwa Mbuye 
wawo. 

39. Ndipo amene atsutsa 
zizindikiro Zathu, ndi agonthi 
ndiponso Abubu, ali mum'dima 
(waumbuli).Amene Mulungu 
wafuna kumlekereraKusokera, 
(amasokera). Ndipo amene 
wamfuna amamuika Panjira 
yolunjika (yomwe Ndi njira ya 
Chisilamu). 

40. Nena: "Tandiuzani ngati 
mazunzo A Mulungu atakufikani 
(pompano Padziko lapansi), 
kapena kukufikani Nthawi 
(yachilango cha tsiku Lomaliza) 
Kodi mudzaitana yemwe Sali 
Mulungu (kuti akupulumutseni)? 
Ngati inu muli oona. 

41. Koma lye yekha ndi Yemwe 
mudzampempha, Ndipo lye 
adzakuchotserani Zomwe 
mukumpempha (kuti 
Akuchotsereni) ngati 
atafuna.Ndipo mudzaiwala zomwe 
mudali Kuziphatikiza (ndi 
Mulungu)." 

42. Ndithu, tidawatumiza 
(Atumiki) kumibadwo yomwe 



^gf^^it^M 












a&rfriii*' 



'?6&&$&4Q&'&J 



wr-v 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



277 V *>i 



*\ fbuty 5jj-* 



idalipo iwe usadadze. Ndipo 
tidawakhaulitsa ndi mazunzo ndi 
masautso kuti iwo adzichepetse 
(pambuyo podzikuza). 

43. Pamene masautso adawafika 
kuchokera Kwa Ife, bwanji 
sadaphunzire Kudzichepetsa? 
Koma mitima yawo Idali youma, 
ndipo SatanaAdawakometsera 
machimo omwe Iwo adali kuchita. 

44. Ndipo pamene adanyozera 
zimene ankakumbutsidwa 
tidawatsekulira Makomo a chinthu 
chilichonse(Chimene adali 
kuchifuna) kufikira Pamene 
adasangalala ndi zomwe 
Adapatsidwa, tidawagwira 
Mwadzidzidzi; pompo adataya 
mtima. 

45. Ndipo mizu ya anthu oipa 
idadulidwa.Kuyamikidwa konse 
kwabwino nkwa Mulungu, Mbuye 
wa zolengedwa. 

46.Nena: "Tandiuzani, ngati 
Mulungu atakuchotserani kumva 
kwanu ndi Kupenya kwanu, 
nadinda chidindo M' mitima yanu 
(kuti asalowemo mawu 
Amalangizo amtundu uliwonse), 
Kodi ndi mulungu uti, kupatula 
Allah, amene angakubwezereninso 
(Zimenezi)?" Taona momwe 
Tikufotokozera mwatsatanetsatane 
Zizindikiro kenako iwo akunyozera. 



*&&!&SM%$i 












Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



278 



V *>i 



*\ pUity 5jj-» 



47. Nena: "Tandiuzani, ngati 
masautso a Mulungu atakufikani 
mwadzidzidzi Kapena moonekera, 
kodi angaonongeke Ndi ena osati 
anthu ochita zoipa? 

48. Ndipo sititumiza atumiki 
koma Kuti akhale ouza nkhani 
zabwino Ndi ochenjeza. Choncho 
amene akhulupirira nakonza 
zinthu,Pa iwo sipadzakhala mantha 
ndiponso Sadzadandaula. 

49. Ndipo amene atsutsa 
zizindikiro Zathu, chilango 
chidzawakhudza Chifukwa 
chakupandukira Kwawo 
chilamulo. 

50. Nena: "Ine sindikukuuzani 
kuti Ndili nazo nkhokwe (za 
zabwino za Mulungu Kotero kuti 
nkukupatsani chimene Mwafuna). 
Ndipo (sindikukuuzani) Kuti 
ndikudziwa zamseri, (Za Mulungu 
kotero kuti nkukufotokozerani 
zomwe zingakufikeni Pamalonda 
anu monga momwe mwafunira 
Kuti ndikuuzeni.) Ndiponso 
Sindikukuuzani kuti ine ndine 
mngelo (Nkumandifunsa kuti, 
"Bwanji Ukudya pomwe uli 
mngelo?") Ine Sinditsata china 
koma zomwe Zikuvumbulutsidwa 
kwa ine. Nena:"Kodi wakhungu 
ndi wopenya Angafanane? Bwanji 
simukuganizira?" 






«jj 



9 >i. 












Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



279 



V frjA-i 



*\ pbuty $jj-> 



51. Achenjeze ndi Qur'an iyi 
omwe Akuopa kuti 
adzasonkhanitsidwa kwa Mbuye 
wawo pomwe ali opanda Mtetezi 
ngakhale muomboli Aliyense 
kupatula lye, kuti iwo aope 
(Mulungu). 

52. Ndipo usawathamangitse 
omwe akupembedza Mbuye wawo 
m'mawa ndi Madzulo pofuna 
chiyanjo chake.Chiwerengero 
chawo sichili pa iwe ngakhale 
pang'ono, ndipo chiwerengero 
chako sichili pa iwo ngakhale 
pang'ono kotero kuti 
Nkwathamangitsa. (Ngati 
uwapirikitsa) Ukhala m'gulu la 
anthu ochita zoipa. 

53. Ndipo momwemo 
tawasankha ena (osauka) Kukhala 
mayeso a ena (olemera) kuti 
(osauka) anene: "Kodi awa ndi 
omwe Mulungu wawasankhira 
ubwino mwa ife (Ndikutisiya ife? 
Hi ndi bodza Sichipembezo 
choona, podziwa iwo ubwino 
Wake ife tisanawudziwe)." Kodi 
Mulungu sadziwa amene 
akumthokoza? 

54. Ndipo (iwe Mneneri) 
akakudzera (awo Osauka) amene 
akhulupirira zizindikiro Zathu 
(atalakwa pang'ono), auze: 
"Mtendere Ukhale pa inu. Mbuye 















Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



280 



V *>i 



*\ ^UuSfl 0jj-*» 



wanu wadzikakamiza Kukhala 
wachifundo kuti mwa inu amene 
achite choipa mwaumbuli, koma 
pambuyo pake nkulapa, nachita 
zabwino, Mulungu 
Amkhululukira; lye Ngokhululuka 
Kwambiri, Ngwachisoni." 

55. Mmenemo ndi momwe 
tikufotokozera Zizindikiro 
mwatsatanetsatane(kuti Choonadi 
chioneke) ndi kuti njira ya oipa 
idziwike bwinobwino. 

56. Nena: "Ine ndaletsedwa 
Kupembedza amene 
Mukuwapembedza kusiya 
Mulungu." Nena: "Sinditsata 
zilakolako zanu; Ndikadatero 
ndikadasokera Ndipo 
sindikadakhala mwa 
Otsogozedwa". 

57. Nena: "Ine ndili ndi 
chisonyezo Chooneka chochokera 
kwa Mbuye wanga (Chotsimikizira 
zomwe ndikunenazi). Koma inu 
mwachitsutsa. Ndilibe(Chilango) 
chimene 

mukuchifulumizitsacho.Palibe 
kulamula koma Nkwa Mulungu. 
Amakamba zoona Zokhazokha; 
lye Ngwabwino Polamula kuposa 
olamula (onse)." 

58. Nena: "Ndikadakhala nazo 
zimene Mukuzifulumizitsazo, 
ndiye kuti Zikadachitika pakati 



8U8&V&1&&$@ 






Z&&S3a* l $l&&&ti& 



@£&&£$\ 












Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



281 



V*>i 



*\ fUuSfi *jj~* 



paine Ndi inu 

(ndikadakakuonongani Koma 
ndilibe nyonga). Ndipo Mulungu 
akuwadziwa bwino anthu Ochita 
zoipa." 

59. Ndipo lye (Mulungu) ali 
nawo Makiyi azobisika palibe 
Akuwadziwa koma lye basi. Ndipo 
Akudziwa zapamtunda ndi za 
Panyanja. Ndipo palibe tsamba 
Limene limagwa koma 
amalidziwa. Ndipo (siigwa) njere 
mumdima wa M'nthaka (koma iye 
akudziwa). Ndipo (sichigwa) 
chachiwisi Ngakhale chouma, 
koma chili M'Buku loonetsa 
chilichonse. 

60. Iye ndiyemwe amakupatsani 
imfa (Yatulo) nthawi yausiku, 
ndipo Amadziwa zimene mwachita 
masana,Kenako amakudzutsani 
usana kuti Ikwane nthawi yanu 
yoikidwa (yofera); Kenako kwa 
Iye ndiko Kobwerera kwanu, 
nadzakuuzani Zimene munkachita. 

61. Iye Ngopambana Yemwe ali 
pamwamba Pa akapolo Ake ndipo 
akutumizirani (Angelo) osunga, 
(olemba zochita Zanu); kufikira 
mmodzi wanu imfa Ikamdzera, 
angelo athuwo amampatsa imfa, 
Ndipo iwo sanyozera (ntchito 
yawo). 

62. Kenako adzabwezedwa kwa 
Mulungu,Mbuye wawo Woona. 



© 



'•• > " v 












W$W2^W%& 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



282 



V^i 



1 pUity 



>J>- 



Dziwani kuti Kuweruza Nkwake. 
lye ngwachangu Powerengera 
kuposa owerengera (onse). 

63. Nena: "Kodi ndani 
Amakupulumutsani M'masautso 
apamtunda ndi panyanja?" 
Mumampempha modzichepetsa 
ndi motsitsa mawu (kuti): "Ngati 
atipulumutsa (m'mazunzo awa,) 
Ndithudi tidzakhala mwa 
othokoza." 

64. Nena: "Mulungu ndi 
Yemwe Amakupulumutsani 
kuzimenezo ndi Kumasautso 
amtundu uliwonse.Kenako inu 
mukumphatikiza (Ndi mafano) 

65. Nena: "lye Ngokhoza 
kukutumizirani Chilango 
kuchokera pamwamba panu 
Kapena pansi pamiyendo yanu, 
kapena Kudzetsa chisokonezo 
(Nkukhala) magulumagulu 
(osamvana), Ndipo (akhoza) 
kuwalawitsa ena ainu Chilango 
chamtopola wa ena." Taona 
Momwe tikufotokozera zizindikiro 
Kuti iwo azindikire. 

66. Koma anthu ako aitsutsa 
Qur'an iyi Pomwe ili yoona. 
Nena: "Ine sindili kapitawo painu." 

67. Nkhani iliyonse (yomwe 
yatchulidwa Apa) ili ndi nthawi 
yake yodziwika (Yofikira). Ndipo 
posachedwapa Mudziwa (izi). 












&&&&&&&& 






a 

'4* 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



283 I V *>» 



1 f Uity 3jj-- 



68. Ndipo (iwe Msilamu 
weniweni) ukawaona omwe 
Akuchita chipongwe ndi aya 
Zathu, apatuke mpaka Anene 
nkhani ina. Ngati Satana 
atakuiwalitsa, (Nkukhala nawo 
pomwe iwo akukambirana Zotere), 
choncho, pambuyo pokumbuka 
usakhale Pamodzi ndi anthu ochita 
zoipa. 

69. Palibe chilichonse chimene 
chingawapeze oopa Mulungu 
chochokera m'chiwerengero cha 
oipawo, Koma chofunika kwa iwo 
(oopa Mulungu) 

Ndikuwakumbutsa (oipawo) kuti 
aope (Aleke zomwe akunenazo). 

70. Asiye amene achita 
chipembedzo Chawo kukhala 
masewera ndi chibwana. Ndipo 
wawanyenga moyo Wadziko 
lapansi. Choncho, akumbutse Ndi 
Qur'aniyo (kuti achenjere), kuti 
Ungaonongedwe mtima uliwonse 
(ndi Kuikidwa m'ndende) 
kupyolera muzomwe Udapata. 
Ndipo sukhala ndi Mtetezi 
ngakhale muomboli posakhala 
Mulungu, ngakhale utayesera 
kupereka Dipo lamtundu uliwonse 
silingavomerezedwe (kwa 
mzimuwo). Awo ndi omwe 
aonongeka ndi kunjatidwa 
Chifukwa chazomwe adapeza. Iwo 
adzakhala ndi chakumwa 



,9 * ,* \9K9l' )i'999* 9 ><• 



OoO 









Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



284 



V»>i 



*\ ^UiSH OjJ-» 



chamadzi a moto kwambiri, ndi 
chilango chopweteka chifukwa cha 
kusakhulupirira Kwawo 
(Mulungu). 

71.Nena: "Kodi tipembedze 
omwe sali Mulungu, omwe 
sangatipatse phindu (Ngati 
titawapembedza), ndiponso 
Sangathe kutivutitsa (tikasiya 
kuwapembedza), Natibwezedwa 
m'mbuyo pambuyo potitsogolera 
Mulungu? tikhale chimodzimodzi 
aja omwe Satana Adawasokeretsa, 
nkukhala achewuchewu Padziko? 
AH nawo anzawo omwe 
akuwaitanira Kuchiongoko (kuti) 
"Bwerani kwathu, (Koma 
samva,sitingakhale monga anthu 
otere)." Nena:"Utsogozi weniweni 
ngwa Mulungu, ndipo 
Talamulidwa kuti tigonjere Mbuye 
wa zolengedwa; 

72. Ndiponso (atiuza kuti:) 
"Pempherani Swala, Muopeni lye 
yemwe kwa lye 
Mudzasonkhanitsidwa." 

73. lye ndiye adalenga Thambo 
ndi nthaka Mwachoonadi. Ndipo 
Panthawi imene akunena 
(Kuchiuza chinthu): 
"Chitika",Ndipo chimachitikadi. 
Mawu ake ndioona. Ndipo Ufumu 
udzakhala Wakewake tsiku limene 
Lipenga lidzaimbidwa. Ngodziwa 












Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



285 V *>i 



% fU^T 



\ i 



jj~* 



zamseri ndi zooneka. lye 
Ngwanzeru zakuya,Wodziwa 
nkhani zonse. 

74. Ndipo (kumbukirani) 
Ibrahim pamene Adauza bambo 
ake, Azara: "Kodi Mukupanga 
mafano kukhala milungu? Ndithu, 
Ine ndikukuonani inu ndi anthu 
anu Kuti muli m'kusokera 
koonekera." 

75. Ndipo momwemo 
tidamuonetsa Ibrahim ufumu 
wakumwamba Ndi pansi (kuti 
ngwa Mulungu)Kuti akhale 
m'modzi mwaotsimikiza. 

76. Ndipo pamene kunam'dera 
adaona nyenyezi.Adati 
(mwadaladala kuti abutse nzeru Za 
opembedza mafano): "(Nyenyezi) 
iyi ndiye Mbuye wanga." Pamene 
idalowa, adati: "Sindikonda 
(Milungu) yomalowa, (yomasowa, 
yakutha)" 

77. Pamene adaona mwezi 
ukutuluka, Adati: u Uyu ndiye 
mbuye wanga." Koma pamene 
udalowa, adati: "Ngati Mbuye 
wanga sandiongolera, 
ndithudi,Ndikhala m'gulu la anthu 
osokera." 

78. Pamene adaona dzuwa 
likutuluka, Adati: "Uyu ndiye 
mbuye wanga; Uyu ngwamkulu 
kwabasi." Koma Pamene lidalowa, 






#3? 















Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



286 



V *>■! 



n f UiSH 5jj-* 



adati: "E inu anthu anga! Ine ndili 
Kutali ndi zomwe 
Mukumphatikiza nazo Mulungu 

79. Ndithu ine ndalungamitsa 
nkhope yanga Kwa yemwe 
adalenga thambo ndi nthaka, 
Ndapendekera kwa lye yekha. 
Ndipo Ine sindili 
mwaom'phatikiza Mulungu Ndi 
mafano. 

80. Ndipo anthu ake 
adakangana naye (Pomuuzakuti: 
"Bwanji ukusiya Chipembedzo 
chamakolo ako; uona Malaulo." 
lye) adati: "Kodi Mukukangana 
nane pa za Mulungu Pomwe lye 
wanditsogolera? Ndipo 
Sindingaope zimene 
mukumphatikiza Naye, kupatula 
Mbuye wanga akafuna Chinthu, 
(apo chiyenera kuchitika). Mbuye 
wanga akudziwa chinthu 
Chilichonse bwinobwino. Nanga 
Kodi simumva ulaliki? (Bwanji 
Simulalikika?") 

81. "Ndipo ndingaope chotani 
zomwe Mwaziphatikiza (ndi 
Mulungu) pomwe Inu simuopa 
kuti mukumphatikiza Mulungu 
(ndi mafano) omwe Mulungu 
Sadawatsitsire pa inu umboni (kuti 
Muziwapembedza). Choncho ndi 
gulu Liti m'magulu awa awiri 
(langa Kapena lanu) loyenera 



©<£$ 



o^3$tf<ji 






fy&\£8tySfrM 






(^*Xj5 



Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



287 



V *>i 



1 fbuSfl OjJ-*» 



koposa Kupeza chitetezo? Ngati 
inu Mudziwa (zinthu). 

82. (Palibe chikaiko kwa) 
amene Adakhulupirira ndipo 
nkusasakaniza Chikhulupiriro 
chawo ndi shiriki (Kupembedza 
mafano), iwowo ali Nacho 
chitetezo. Ndiponso iwo Ndi 
omwe ali oongoka. 

83. Ndipo izi ndi (zina mwa) 
zizindikiro Zathu (mitsutso yathu), 
zomwe Tidampatsa Ibrahim pa 
anthu ake. Timamtukulira 
ulemerero amene Tamfuna. 
Ndithu, Mbuye wako Ngwanzeru 
zakuya, Ngodziwa Kwambiri. 

84. Ndipo tidampatsa (Ibrahim 
mwana Wotchedwa) Isihaka ndi 
(mdzukulu Wotchedwa) Yakubu. 
Onse tidawaongola. Nayenso Nuhi 
tidamuongola kale (Asadadze 
Mneneri Ibrahim). Ndipo 
Kuchokera m'mbumba yake (Nuhi, 
Tidamuongola) Daudi, Sulaiman, 
Ayubu, Yusufu, Musa, ndi 
Haaruna. Ndipo umo ndi momwe 
Timawalipirira ochita zabwino. 

85. Tidamutsogoleranso 
Zakariya, Yahaya, Isa ndi Illiyasi. 
Onse adali mwa Anthu abwino. 

86. Ndi Ismail, Elisha, Yunusu 
(Yona) ndi Luti (Loti). Onsewa 
tidawapatsa Ubwino pazolengedwa 
(pa anthu). 


















Surat 6. AI-An'am Juzu 7 



288 V >> 



*\ f Uity Sjj-" 



87. (Ndiponso tidawatsogolera) 
Ena mwa atate awo, Ana awo ndi 
abale awo. Ndipo tidawasankha 
ndi Kuwaongolera ku Njira 
yolunjika. 

88. Ichi ndi chiongoko cha 
Mulungu. Ndi icho akuongolera 
yemwe wamfuna Mwa anthu ake 
(chifukwa Chosamphatikiza ndi 
mafano).Akadakhala kuti 
(aneneriwo)Adamphatikiza (ndi 
zina) Zikadawaonongekera zimene 
ankachita. 

89. Iwo ndi omwe tidawapatsa 
mabuku, Chiweruzo, ndi uneneri. 
Ngati Awa osakhulupirira azikane 
izi, Basi, tazipereka kale kwa 
Anthu omwe sangazikane. 

90. Iwo ndi omwe Mulungu 
adawaongola Choncho, tsatira 
chiongoko chawo. Nena: 
"Sindikukupemphani malipiro 
Paizi (zomwe 

ndikukuphunzitsanizi, Koma 
ndikungotumikira Mulungu). Ichi 
sichina koma ndi ulaliki kwa 
Zolengedwa (majini ndi wanthu). 

91. Koma (Ayuda) 
sadamulemekeze Mulungu monga 
momwe zikufunikira 
Pomulemekeza pomwe adati: 
"Mulungu Sadavumbulutsepo 
chilichonse kwa munthu 
Aliyense." (Adanena izi pamene 












& 









Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



289 V ^ 



\ fUity Ojj-*. 



mtumiki Adawauza kuti Qur'an 
ndi buku lomwe Mulungu 
wavumbulutsa). Nena: "Kodi 
ndani Adavumbulutsa Buku 
lomwe lidadza ndi Musa? Lomwe 
lidali kuunika ndi chiwongoko 
kwa Anthu, lomwe mwalipanga 
kukhala zigawo-Zigawo; zimene 
mwafuna kuonetsa kwa anthu 
Mukuzionetsa. Koma zambiri 
mukubisa (zomwe Sizigwirizana 
ndi zofuna zanu).Ndipo 
Mwaphunzitsidwa (ndi iyi Qur'an) 
zomwe Simudali kuzidziwa, inu 
ngakhale makolo anu. Nena: 
"Mulungu (ndi Yemwe 
wavumbulutsa Iyi Qur'an ndi 
mabuku ena" ) .Kenako asiye 
Azingosewera m'kubwebweta 
kwawo (Kopanda pake). 

92.Ndipo iyi Qur'an ndi Buku 
limene Talivumbulutsa lamadalitso 
ochuluka; Ndipo likutsimikizira 
zomwe Zidalitsogolera. Ndikuti 
uchenjeze Anthu a'mchimake cha 
mizinda (Makka) ndi anthu omwe 
ali M'mphepete mwake. Ndipo 
Amene akukhulupirira tsiku 
Lomaliza, akulikhulupirira 
(Bukuli). Ndipo iwo Swala Zawo 
akuzisunga bwino. 

93. Kodi ndani woipitsitsa 
koposa yemwe Wampekera bodza 
Mulungu kapena wonena: 
"Wandininkha" (chivumbulutso) 















Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



290 



V^jJH 



*\ fbuSM $j>-> 



pomwe Sichidavumbulutsidwe 
Kwa iye chilichonse; ndiyemwe 
Akunena: "Ndivumbulutsa monga 
chimene Mulungu wavumbulutsa." 
Ukadawaona anthu Ochita zoipa 
akuthatha ndi imfa, nawo angelo 
atawatambasula manjaawo 
(ndikuwauza:) "Tulutsani moyo 
wanu; lero mulipidwa Chilango 
chonyozeka chifukwa cha Zomwe 
mudali kunenera Mulungu 
popanda choonadi, Ndi 
kudzitukumula kwanu pa 
Zizindikiro zake". 

94. Ndipo (tsiku lakiyama 
tidzakuuzani): "Ndithudi, 
mwatidzera mmodzimmodzi 
(Payekhapayekha popanda chuma 
ndi Ana kuti akupulumutseni), 
monga mmene Tidakulengerani 
pachiyambi. Ndipo mwasiya 
Kumbuyo kwanu zonse zomwe 
tidakupatsani. Ndipo sitikuona 
pamodzi nanu apulumutsi anu aja, 
Amene munkati ngothandizana 
(ndi Mulungu; ndi Kuti iwo ndi 
apulumutsi anu). Ndithudi 
(mgwirizano) Omwe udali pakati 
panu waduka. Ndipo Zakutaikirani 
zimene Munkaziganizira (kuti ndi 
milungu)." 

95. Ndithu Mulungu ndi 
Yemwe amang'amba njere Ndi 
mbewu ya zipatso (kuti imere). 
Amatulutsa chamoyo m'chakufa. 















Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



291 V ,>' 



n f UiSfi 3j>-» 



Ndiponso ngotulutsa chakufa 
m'chamoyo. Ameneyu ndi 
Mulungu. Nanga 
Mukutembenuzidwa chotani? 

96. lye ndi Yemwe ali 
Wotsekula M'bandakucha, ndipo 
amaupanga Usiku kukhala wabata 
(nthawi Yopumula) ndi dzuwa ndi 
mwezi Kukhala zowerengera 
[masiku ndi zaka (Kalendala)]. 
Ichi nchikonzero cha Wamphamvu 
zoposa, Wodziwa kwambiri. 

97. lye ndi amene 
anakupangirani Nyenyezi kuti 
zikutsogolereni (Njira) mum'dima 
wapamtunda ndi panyanja. Ndithu 
talongosola Mokwanira zizindikiro 
(zathu) Kwa anthu odziwa 

98. Ndipo lye ndi yemwe 
adakulengani Kuchokera mu 
mzimu umodzi. (Kwa inu) alipo 
malo okhalapo (dziko Lapansi 
kapena m'mimba mwa Mayi) 
ndiponso posungirapo (Mmanda 
kapena munsana mwa bambo) 
Ndithu, tafotokoza zizindikiro 
(Zathu) kwa anthu ozindikira. 

99. lye ndi Yemwe 
amavumbwitsa mvula Kuchokera 
kumwamba. Ndi madzi a mvulayo 
timameretsa Mmera wachinthu 
chilichonse. Ndipo m'menemo 
Tikuphukitsa masamba obiriwira, 
Ndipo mum'mera umenewo 



%$m 


















Siirat 6. Al-An'am Juzu 7 



292 



V *>i 



*\ ^bwVl Ojj~- 



tikutulutsa Mkati mwake njere 
zosanjikana; Ndiponso m'kanjedza 
m'mikoko Mwake (Mumatuluka) 
maphava ogoweka (Ndizipatso). 
Ndipo amakumeretserani Minda 
yampesa, mzitona ndi 
Makomamanga, ofanana ndi 
osafanana. Tapenyani zipatso zake 
pamene Zikupatsa ndi kupsa 
kwake. Ndithu, m'zimenezo Muli 
zizindikiro Kwa anthu 
okhulupirira. 

100. Ndipo (pamwamba pa 
izi)Anthu ampangira Mulungu 
ziwanda Kukhala zinzake,pomwe 
lye ndi Yemwe adazilenga.Ndipo 
akumnamizira Kuti ali ndi ana 
aamuna ndi aakazi Popanda 
kudziwa. Ali kutali 
Wolemekezekayo,Ndipo 
Watukuka kuzimene Akusimbazo. 

101. lye ndiye Mlengi 
wathambo Ndi nthaka, zingatheke 
bwanji Kukhala ndi mwana 
pomwe lye alibe mkazi? Ndipo 
Ndi Yemwe adalenga chinthu 
Chilichonse.Ndiponso lye 
Ngodziwa chinthu chilichonse. 

102. Ameneyu ndi Mulungu, 
Mbuye Wanu; palibe wina woti 
nkumpembedza Mwachoonadi 
koma lye. Mlengi wachinthu 
chilichonse . Choncho, 
mpembedzeni. lye ndi Muyang'aniri 
wachinthu chilichonse. 






4. 















Surat 6. Al-An'am Juzu 7 



293 



v tjA-i 



*; fbuSfi Sj>-> 



103. Maso samufika (kuti 
nkumuona); koma lye amawafika 
maso (amawaona pamodzi Ndi eni 
masowo). lye Ngodziwa Zobisika 
kwambiri ndi zoonekera 

104. "Ndithu umboni 
wotsimikizika Wakufikani 
kuchokera kwa Mbuye 
Wanu,choncho amene atsekule 
maso ake Nkuyang'ana ndiye kuti 
Zotsatira zake zabwino zili pa iye 
Mwini. Ndipo amene akhale 
wakhungu Zili pa iye mwini. 
Ndipo ine Sindili kapitawo wanu." 

105. Motero tikulongosola 
mwatsatanetsatane Zizindikiro, 
(kuti azindikire). Ndipo anena 
kuti:"Wachita kuphunzira (izi, si 
Mulungu amene Wakuuza" Ndipo 
tazibwerezabwereza chonchi) Kuti 
tilongosole ndi kufotokoza 
Momveka kwa anthu odziwa. 

106. Tsata zimene Mbuye wako 
wakuvumbulutsira. Palibe 
Wopembedzedwa mwachoonadi 
Koma Iye. Ndipo ape we 
Amushirikina. 

107. Ndipo Mulungu akadafuna 
Sakadamphatikiza (ndi mafano) 
Ndipo sitidakuike pa iwo kukhala 
Muyang'aniri wawo. Ndipo iwe 
suli Muyimiliri wawo. 

108. Ndipo usawatukwane 
amene akupembedza (Mafano) 















C 'l*£ 9 < t »f, '^*\\> 9 < 









^I^&u%t2$!i!5£ 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



294 



A tjJrl 



1 ^OuSfl Ojj-*» 



kusiya Mulungu, kuopera Kuti 
angamtukwane Mulungu 
mwamwano Popanda kuzindikira. 
Motero Tawakometsera anthu onse 
zochita Zawo. Potsiriza 
adzabwerera Kwa Mbuye wawo, 
choncho, lye adzawauza zonse 
zomwe Adali kuchita. 

109.Ndipo (Akafiri) adalumbira 
Mulungu ndi Malumbiro 
amphamvu kuti ngati 
Adzachikhulupirira. Nena: 
"Zozizwitsa Zili kwa Mulungu 
(sizili m'manja mwanga). Kodi 
nchinthu chanji 

chingakudziwitseni (Inu Asilamu) 
kuti (ngakhale) chidze 
(Chozizwitsacho) iwo 
sangakhulupirire? 

HO.Ndipo titembenuza Mitima 
yawo ndi maso awo (Kotero kuti 
sangathe kuchikhulupirira 
Ngakhale atachiona 
chozizwitsacho) Monga momwe 
sadaikhulupirire (Qur'an) 
Poyamba ndipo tiwasiya 
Akuyumbayumba m'machimo awo. 

111. Ndipo ngati 
tikadawatumizira Angelo (Kuti 
adzaikire umboni za uneneri 
Wako), ndipo akufa 
nkuwayankhula, (Naonso 
nkuvomereza kuti izi Nzoona; 
kuonjezera apo) 
Nkuwasonkhanitsira chinthu 



^i^^aniS 



i«Wi 



*Wr*" 



9'< 















Surat 6. Al-An 4 am Juzu 8 



295 



A *>i 



% fUuVl 5jj~» 



Chilichonse pamaso pawo, 
Sakadakhulupirira pokhapokha 
Mulungu akadafuna Koma ambiri 
a iwo ngosazindikira. 

112.Ndipo nchomwechi 
tidamuikira Adani mneneri 
aliyense (omwe) Ndi asatana a 
muanthu ndi asatana A 
m'ziwanda,( omwe) 
amadziwitsana Wina ndi mnzake 
mawu okometsa Ncholinga 
chonyenga.Ndipo Mbuye wako 
Akadafuna, sakadatha kuchita 
zimenezi Choncho asiye ndi 
zimene akupeka 

113. Ndi kuti ipendekere 
kumawu amenewo Mitima ya 
anthu osakhulupirira Tsiku la 
chimaliziro, ndi kuyanjana Nawo 
(mawu) ndikutinso apeze 
(Machimo) omwe amawapeza. 

114.(Nena:)"Kodi ndifune 
woweruza Wina kusiya Mulungu, 
pomwe lye Ndi Yemwe 
adavumbulutsa Buku kwa inu 
Lofotokoza chilichonse?" Ndipo 
Omwe tidawapatsa Buku 
Akudziwa kuti (Qur'an) 
yavumbulutsidwa Ndi Mbuye 
wako mwachoonadi. Choncho, 
usakhale mwaokaikira. 

115. Ndipo mawu a Mbuye 
wako akwanira Moona ndi 
mwachilungamo. Palibe Amene 















rt'^r^i *w* 9'\$ 9 <C" 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



296 



A ftji-l 



n £ liu^i 5jj-* 



angathe kusintha mawu Ake. lye 
Ngwakumva, Ngodziwa. 

116.Ngati umvera ambiri 
amene ali Padziko lapansi, 
akusokeretsa Panjira ya Mulungu. 
Satsatira Koma zakungoganizira. 
Ndipo Sali chilichonse koma 
Akungonama 

117.Ndithu, Mbuye wako ndi 
Yemwe Akudziwa bwino amene 
asokera Ku njira Yake, ndiponso 
lye Akudziwa bwino za oongoka. 

118. Choncho, idyani (nyama) 
zomwe Dzina la Mulungu 
latchulidwapo (Pozizinga osati zofa 
zokha), Ngati inu mukhulupiriradi 
aya(zizindikiro) zake. 

119.Mungasiirenji kudya 
(nyama) imene Poizinga dzina la 
Mulungu Latchulidwapo, pomwe 
wakufotokozerani Momveka 
chomwe wachiletsa Kwa inu, 
kupatula (mukadya 
choletsedwacho) Mosimidwa ndi 
kukakamizidwa (Chifukwa cha 
njala)? Koma ndithu ambiri 
Akusokeretsa (ena) mwazifuniro 
zawo Popanda kudziwa. Ndithu 
Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa 
bwino za Olumpha malire. 

120. Siyani machimo oonekera 
ndi Obisika. Ndithu, amene achita 
Machimo adzalipidwa chifukwa 
Cha zomwe adali kuchita (Zoipa). 






>"''JLA" 






Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



297 



AtjJrl 



■\ pbu^Il Sjj~- 



121. Ndipo musadye (nyama) 
imene Yazingidwa popanda 
kutchula Dzina la Mulungu. 
Kutero ndikuchimwa. Ndithudi, 
asatana amanong'onezera 
Abwenzi awo kuti akangane ndi 
inu (M'zinthu zonga zimenezi). 
Ngati Muwamvera, ndiye kuti 
mukhala Amushirikina. 

122. Kodi yemwe adali wakufa, 
Kenako nkumuukitsa ndi 
kumpangira Kuunika; choncho ndi 
kuunikako Nkumayenda kwa 
anthu, kodi Angafanane ndi 
yemwe chikhalidwe Chake chili 
mumdima (wa umbuli) Ndipo 
sakutha kutuluka m'menemo? 
Motero zakometsedwa kwa 
Osakhulupirira (zoipa) zomwe 
akhala akuchita. 

123. Chomwechonso tidaika 
mmudzi uli wonse Akuluakulu 
owonongamo kuti Azichitamo 
ndale (zoletsa anthu Kuyenda pa 
njira ya Mulungu). Ndipo ndale 
zawo sizipweteka Aliyense koma 
iwo eni, koma sazindikira. 

124. Ndipo chizindikiro 
chikawadzera, Amati: 
"Sitikhulupirira, mpaka Tipatsidwe 
monga zomwe atumiki A Mulungu 
adapatsidwa." Mulungu Ndi amene 
akudziwa pamalo pomwe Akuika 
uneneri wake, (sikuti 
Angapatsidwe munthu aliyense). 















Surat 6. Al-An'am Juzu 8 I 298 1 * *j*-i 



*\ fbuSfl 5jj^ 



Posachedwa kunyozeka kochokera 
Kwa Mulungu ndi chilango 
choopsa Ziwafika amene achita 
zoipa Chifukwa chandale zawo 
zomwe akhala Akuchita. 

125. Choncho, amene Mulungu 
akufuna Kumuongola, 
amamtsekula chifuwa Chake kuti 
Chisilamu chilowemo Ndipo 
yemwe Mulungu akufuna 
kumulekerera Kusokera 
amachichita chifuwa chake 
kukhala Chobanika, chovutika 
kwambiri (Kutsata Chisilamu) 
ngati kuti akukwera Kumwamba. 
Umo ndi momwe Mulungu 
Akuwaunjikira uve anthu omwe 
sakukhulupirira. 

126. Ndipo iyi (Chipembedzo 
cha Chisilamu) Ndi njira ya 
Mulungu yoongoka. Ndithu, 
Tazifotokoza zizindikiro momveka 
kwa Anthu okumbukira. 

127. (Anthu abwino) adzapeza 
nyumba Yamtendere kwa Mbuye 
wawo. lye Ndi Mtetezi wawo, 
chifukwa Cha zomwe adali 
kuchita. 

128. Ndipo (akumbutse) tsiku 
limene Adzawasonkhanitsa onse 
(Nkuwauza): "E inu khamu la 
ziwanda! Ndithudi, Mudatenga 
okutsatirani ambiri mwa anthu 
(Powasokoneza)."Ndipo abwenzi 















Siirat 6. Al-An'am Juzu 8 



299 I A*j*-» 



*\ pwty 5jj~* 



awo mwa Athu adzati: "Mbuye 
wathu! Tidali kupindulitsana. 
Pakati pathu Ndipo tsopano 
taifikira Nyengo yathu imene 
mudatiikira." (Mulungu) adzati: 
"Malo anu ndi Kumoto. 
Mukakhala m'mmenemo Muyaya, 
pokhapokha Mulungu Akafuna." 
Ndithu, Mbuye wako Ngwanzeru 
zakuya, Ngodziwa kwambiri. 

129. Chomwechi timaika 
chimvano pakati pawochita zoipa 
chifukwa cha machimo omwe 
adali kupeza Kuchokera m'zochita 
zawo zoipa). 

130. (Tsiku la Kiyama 
adzafunsidwa): "E inu magulu a 
ziwanda ndi anthu! Kodi 
sadakudzereni atumiki ochokera 
Mwa inu, amene 
amakufotokozerani Zizindikiro 
zanga, nakuchenjezani Zokumana 
ndi tsiku lanu ili?" Adzati : 
"Tadziikira umboni tokha." Ndipo 
moyo Wadziko lapansi 
udawanyenga. Ndipo adzaziikira 
Okha umboni kuti iwo Adali 
osakhulupirira. 

131. Zimenezi nchifukwa choti 
Mbuye wako Sali woononga midzi 
mwachinyengo pomwe Eni ake ali 
oiwala. (Koma ankawatumizira 
aneneri Kuti awachenjeze ndi 
kuwakumbutsa). l 



©' 












Mulungu sapereka chilango kwa anthu asanawatumizire Mtumiki. Ndiponso 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



300 



A *jA-i 



*\ pUity i^y* 



132. Ndipo onse adzakhala ndi 
maudindo (Aulemerero) kuchokera 
m'zochita zawo. Ndipo Mbuye 
wako sali Wamphwayi pa zimene 
akuchita. 

133. Ndipo Mbuye wako 
Ngokwanira (Wolemera), Mwini 
chifiindo. Ngati afuna 
Angakuchotseni ndi kuwaika 
m'malo Mwanu amene wawafuna 
monga momwe Adakulengerani 
kuchokera m'mbumba Ya anthu 
ena. 

134. Ndithu, (palibe chikaiko) 
Zomwe mukulonjezedwa, Zifika. 
Ndipo simungathe kuzilepheretsa. 

135.Nena: "E inu anthu anga! 
Chitani Zanu (zimene mufuna) 
momwe Mungathere. Nanenso 
ndichita zanga. Choncho 
mudzaziwa kuti ndani Mapeto ake 
adzakhale ndi malo Abwino. 
Ndithudi, sangapambane Anthu 
ochita zoipa." 1 

136. Ampangira Mulungu 
(amugawira) gawo M'zomera ndi 
ziweto zimene (Mulungu) 















sangawalange pa zinthu zomwe nzosatheka kuzizindikira, pokhapokha Mtumiki 
atawaphunzitsa, monga kupemphera Swala, kusala pa mwezi wa Ramadhani. 
Koma angawalange pazomwe iwo angathe kuzizindikira kuti nzoipa; monga 
munthu kumchenjerera mnzake ndi zina zotero. 

1 Aya iyi ikusonyeza kuti munthu wapatsidwa ufulu wochita kapena kusachita 
poopera kuti angadzanene kuti adakakamizidwa. Apa nzachidziwikire kuti 
amene wasankha chabwino adzapeza chabwino. Ndipo yemwe wasankha 
choipa adzapeza choipa. 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



301 



A *jJUi 



■\ ^toSh 5jj-- 



Adalenga. Akunena: "Gawo ili ndi 
La Mulungu,"mkuyankhula 
kwawo Kwachabe, "Ndipo gawo 
ili ndi La aja omwe 
tikuwaphatikiza ndi Mulungu." 
Choncho zomwe alinga Kuwapatsa 
aphatikizi awo, sizingafike Kwa 
Mulungu. Ndipo zimene zili Za 
Mulungu, ndi zomwe zingafike 
Kwa aphatikizi awo (mafano awo): 
Kwaipitsitsa kuweruza kwaoku. 1 

137. Momwemo milungu 
(mafano) yawo Imawakometsera 
ophatikiza Mulungu ndi Mafano 
kupha ana awo (monga Nsembe ya 
mafanowo) kuti awaononge 
Ndikuwabweretsera chisokonezo 
Pachipembezo chawo. Ndipo ngati 
Mulungu Akadafuna, sakadachita 
zimenezo. Choncho Asiye ndi izo 
zomwe akupeka. 

138. Iwo akuti: "Ziweto izi ndi 
mbewu izi, Nzoletsedwa; palibe 
angazidye koma Amene tawafuna 
(kuti adye)" zonsezi Mkuyankhula 
kwawo kwachabe. Ndipo 












Kale anthu osakhulupirira pamene ankalima akafuna kubzala, minda yawo 
adati kuigawa zigawo ziwiri. Ankati "Mbewu zachigawo ichi nza Mulungu, kuti 
mbewu zakezo adzazigwiritsa ntchito powapatsa masikini, ana a masiye ndi 
osowa. Ndipo ankatinso "Mbewu zachigawo ichi nzamafano athu omwe ankati 
ngamnzake a Mulungu kuti zinthu zotuluka m'menemo ziperekedwe kwa 
anthu ogwira ntchito m'menemo. Choncho ngati patapezeka mliri pachigawo 
chomwe ankati zokolola zake nzamafano awo, amatenga chigawo chomwe 
amati dzinthu dzake nza Chauta napereka kumafano. Koma mliri ukagwera 
pa chigawo cha Mulungu, sadali kutenga zamafano nkupereka kwa Mulungu. 
Izi amachita ngati mafano ngabwino kuposa Mulungu. 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



302 



A *>l 



n f\*jH\ *jj-- 



(Amanenanso): "Ziweto izi, misana 
yake Njoletsedwa (kuikwera)." 
Ndipo paziweto zina satchula 
dzina la Mulungu pozizinga;- 
kungompekera Bodza lye. Ndipo 
posachedwa Adzawalipira pa 
zomwe adali kupeka. 

139. Ndipo amanenanso: 
"Zimene zili M'mimba Mwa 
ziweto izi, ndi za amuna okha; 
Ndipo nzoletsedwa kwa akazi 
athu". Koma ngati chili chibudu, 
onse Adali kugawana (amuna ndi 
akazi). Ndithudi, adzawalipira ndi 
zonena zawozo. Ndithu lye 
Mulungu),Ngwanzeru zakuya, 
Wodziwa kwambiri. 

140. Ndithu, adaluza amene 
adapha ana awo Mwaumbuli 
popanda kudziwa, Ndi kuletsa 
(chakudya) chimene Mulungu 
awapatsa, pakungompekera Bodza 
Mulungu. Ndithu adasokera ndipo 
Sadali oongoka. 

141. Ndipo Iye( Mulungu) ndi 
amene adapanga Minda (ya 
mitengo) yothaza Ndi yosathaza; 
ndipo (Adapanga) mitengo 
yakanjedza ndi Mmera wazipatso 
zosiyanasiyana makomedwe Ake 
ndipo adapanganso mzitona ndi 
Makomamanga, zofanana 
(mmaonekedwe) ndi Zosiyana 
(mmakomemedwe). Idyani zipatso 
zake Pamene zikupatsa. Ndipo 



<&'!>* VrtKB't''. »_! .*''*f<' 



jp&&&k g$ tx£ $% 






"'($' \ 9 h\''' 9 ~'\\<\'i "h 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



303 A *> 



*\ fbuty «jj-> 



perekani Chopereka chake tsiku 
lokolola (Powapatsa masikini ndi 
ogundizana Nawo nyumba). Ndipo 
musaziononge Pakudya mopyoza 
muyeso. Ndithu, lye (Mulungu) 
sakonda opyoza muyeso. 

142. Ndipo m'gulu la nyama, 
(Mulungu adalenga ) Zonyamulira 
katundu ndi zopangira choyala 
(Bweya bwake). Idyani zimene 
Mulungu wakupatsani ndipo 
musatsate Mapazi a Satana (ndi 
abwenzi ake Pozichita halali 
kapena haramu Zomwe Mulungu 
sadalamule. Satana Sakufunirani 
zabwino); Ndithu iye Ndi mdani 
wanu woonekera. 

143. (Adakulengerani) mitundu 
isanu Ndi itatu yanyama 
(pophatikiza Zazimuna ndi 
zazikazi); Nkhosa (adalenga) 
ziwiri (Yaimuna ndi yaikazi); 
mbuzi (Adalenga) ziwiri (yaimuna 
ndi Yaikazi). Nena: "Kodi Iye 
Adakuletsani zazimuna zonse 
Ziwiri, (mbuzi ndi nkhosa) Kapena 
zazikazi ziwiri, (Nkhosa ndi 
mbuzi), kapena zomwe Zili 
m'mimba mwa zazikazi Ziwirizo? 
Ndiuzeni mwanzeru ngati 
Mukunenazi nzoona (kuti 
Mulungu Adatero). 

144. Ndipo (adalenganso) 
ngamira ziwiri, (Yaikazi ndi 
yaimuna). Ng'ombe 



U^$&3*>m£>i 









b *"». . CJil ' ' »'\ 






Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



304 



A *j*-i 



1 flAiSll 3jJ-*> 



(Adalenganso) ziwiri, (yaimuna 
Ndi yaikazi). Nena: "Kodi (lye) 
Adakuletsani zazimuna zonse 
ziwiri (Ngamira ndi ng'ombe), 
kapena zazikazi Zonse ziwiri 
(ngamira ndi ng'ombe), Kapena 
zomwe zili m'mimba mwa 
Zazikazi ziwirizo? Kodi mudali 
Mboni pamene Mulungu 
ankakulamulani izi? Kodi ndi 
ndani woipitsitsa kuposa amene 
Akupekera bodza Mulungu kuti 
asokeretse Anthu popanda 
kudziwa (Malamulo A Mulungu)?. 
Ndithu, Mulungu saongola Anthu 
ochita zoipa. 

145. Nena: "Sindikupeza 
m'zimene Zavumbulutsidwa kwa 
ine choletsedwa ( kudya) Kwa 
yemwe akufuna kudya. 
Pokhapokha chikakhala chakufa 
chokha, Kapena liwende lomwe 
limachucha, Kapena nyama ya 
nkhumba; chifukwa Chakuti 
zonsezi ndi uve (ndiponso Kudya 
zotere) ndiko kutuluka 
M'chilamulo cha Mulungu. 
Kapena (Nyama) yozingidwa 
popanda Kutchulapo dzina la 
Mulungu. Koma Amene 
wasimidwa (nkudya zoterezi) 
Popanda kukonda kapena kupyoza 
Malire, ndithu, Mbuye wako 
Ngokhululuka Kwambiri, 
Ngwachisoni. (Wotere 
Amamkhululukira) . 









Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



305 



A*>i 



*\ fUJ 5 ^ Qjj** 



146. (Izi ndi zomwe 
takuletsani). Naonso Ayuda 
tidawaletsa kudya Nyama iliyonse 
yokhala ndi zikhadabu Ndipo 
ng'ombe ndi mbuzi tidawaletsa 
Kudya mafuta ake kupatula mafuta 
Omwe misana yake yasenza, 
kapena Okhala m'matumbo, 
kapena omwe Asakanikirana ndi 
mafupa. Tidawalipira izi chifukwa 
cha machimo Awo. Ndithu, Ife 
ndioona (pazomwe Tikunenazi). 

147.Ngati akukutsutsa 
(pazimene Zavumbulutsidwa), 
auze (Mowachenjeza): "Mbuye 
wanu (Yemwe ngofunika 
kum'khulupirira Ndi kutsatira 
malamulo ake), Ngwachifundo 
chambiri (kwa yemwe 
Akumumvera, ndi yemwe 
akumunyoza Pano padziko 
lapansi). Komatu Chilango chake 
sichibwezedwa Kwa anthu oipa." 

148. Amene akuphatikiza 
(Mulungu ndi Mafano) anena: 
"Ngati Mulungu Akadafuna, 
sitikadam'phatikiza, Ife ngakhale 
makolo athu. Ndipo Sitikadaletsa 
chilichonse. (Choncho, Izi zomwe 
tikuchita, Mulungu Akuziyanja). 
Momwemonso adatsutsa Omwe 
adalipo patsogolo pawo Kufikira 
adalawa chilango chathu. Nena: 
"Kodi muli nako kudziwa (koku- 
Tsimikizirani zimenezi)? Koti 












Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



306 



A*j*-l 



n fW*iii 3jj-- 



mungatitulutsire. (Umboni wake 
wotsimikizira kuti Mulungu 
Adakulamulani zimenezi)? Inu 
simutsatira China, koma 
zongoganizira basi. Ndipo 
Simukunena china koma zabodza 
basi." 

149.Nena: "Mulungu ndi 
Yemwe ali ndi Umboni 
wokwanira.Choncho akadafuna, 
Akadakuongolani nonsenu." 

ISO.Nena: "Tabweretsani 
mboni zanuzo Zomwe zingapereke 
umboni kuti Mulungu adaletsa izi. 
Ndipo ngati Zitapereka umboni, 
(mboni zawozo) usaikire Nawo 
umboni pamodzi Ndi iwo. Ndipo 
usatsate zofuna Za omwe atsutsa 
zizindikiro zathu Ndi amene 
sakhulupirira tsiku Lomaliza; 
omwenso akufanizira Mbuye 
wawo ndi milungu yabodza. 

lSl.Nena: "Idzani kuno, 
ndikuwerengereni Zomwe Mbuye 
wanu wakuletsani." 
Musamphatikize Ndi chilichonse, 
ndipo achitireni Zabwino makolo 
anu; musaphe ana Anu chifukwa 
chakuopa umphawi; Ife tikupatsani 
riziki inu pamodzi Ndi iwo; 
musayandikire Zoyipa, zoonekera 
ndi zobisika; ndipo Musaphe 
munthu yemwe Mulungu adaletsa 
(Kumupha) kupatula ikapezeka 















Surat 6. AI-An'am Juzu 8 



307 



A*>i 



% pUiSf* *jj~» 



njira Yoyenereza (kumupha). 
Akukulangizani Izi kuti muziike 
mu nzeru zanu. 

152.Ndipo musachiyandikire 
chuma cha Ana amasiye, koma 
m'njira yabwino (Monga 
kuchichulukitsa ndi malonda) 
Mpaka afike pamsinkhu 
wokwanira. Ndipo kwaniritsani 
mwachilungamo Miyeso yambale 
ndi masikelo; Sitikakamiza 
munthu koma chimene Angathe; 
ndipo pamene mukunena, 
(popereka Umboni), nenani 
mwachilungamo ngakhale 
(Umboniwo) uli wokhudza 
achibale. Ndipo kwaniritsani 
lonjezo la Mulungu. Izi ndi zomwe 
akukulangizani Kuti 
mukumbukire. 

153. (Auze kuti) ndithu, iyi ndi 
njira yanga Yoongoka. Choncho 
itsateni. Ndipo musatsate Njira zina 
zambiri kuopera kuti Zingakuikeni 
kutali ndi njira Yake, (Mulungu) 
wakulangizani izi kuti Mudziteteze 
kuzoipa. 

154. Ndipo Musa tidampatsa 
Buku (kukhala) Lokwaniritsa 
(chisomo) kwa yemwe Wachita 
zabwino, lofotokoza chinthu 
Chilichonse, chiongoko ndi 
Chifundo, kuti iwo akhulupirire Za 
kukumana ndi Mbuye wawo. 









J» i^ • 9 <r 






t "Z 'J > -'"fey 9 >'\'\ 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



308 



A *>i 



T, ^UiSfl 3j_^j 



155.Ndipo iyi (Qur'an) ndi 
Buku lodalitsika Lomwe 
talivumbulutsa (kwa inu), 
Choncho, litsateni ndi kuopa 
(Mulungu) kuti muchitiridwe 
Chifundo; 

156. Kuti musadzanene (tsiku la 
Kiyama) Kuti: "Mabuku 
adavumbulutsidwa Pamagulu awiri 
omwe adalipo Patsogolo pathu, 
(Ayuda ndi Akhrisitu); ndipo ife 
sitidadziwe Chilichonse pazomwe 
adali kuwerenga Ndi kuphunzira;" 

157. Kapena kuti musadzati: 
"Likadavumbulutsidwa Buku kwa 
ife, ndithudi, Tikadakhala oongoka 
kuposa iwo." Choncho, 
chakudzerani chizindikiro 
Kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi 
Chiongoko ndi mtendere. Kodi 
Ndani woipitsitsa kwambiri 
kuposa Amene watsutsa 
zizindikiro za Mulungu ndi 
kutembenukira kutali Nazo? 
Tidzawalipira amene 
akutembenukira kutali ndi 
zizindikiro zathu, Chilango choipa, 
chifukwa chakudziika Kwawo 
kutali. 

158. Kodi chilipo chimene 
akudikira Kuposa kuwadzera 
angelo (Kudzawachotsa miyoyo 
yawo?) Kapena kudza Mbuye 
Wako?(Tsiku la Kiyama 
kuzaweruza) Kapena kudza zina 






^ssyauJi; 4 *' 






-»i.n * . ." 



\j>€t*}» 



«Vx s^J 



Ooo^j fid c^j yVuo (^j 






Surat 6. AI-An'am Juzu 8 



309 



A *>l 



1 f\*j^\ Qjj~> 



mwa Zizindikiro za Mbuye wako 
(zomwe Adati zidzadza)? Tsiku 
lakudza Zina mwazizindikiro za 
Mbuye wako, Munthu 
(wosakhulupirira) Chikhulupiriro 
chake (panthawiyo) 
Sichidzamthandiza, yemwe 
sadakhulupirirepo kale, kapena 
(Msilamu) Yemwe sanapindule 
nacho Chikhulupiriro chake. Nena: 
" Dikirani. Nafenso tikudikira." 1 

159.Ndithudi, anthu amene 
achigawa Chipembedzo chawo, 
nakhala Mipingomipingo, iwe 
Siuli nawo pachilichonse. Ndithu, 
zotsatira zawo zili kwa Mulungu, 
(ndi yemwe adzawalanga. Ndipo 
panthawi yowalanga) adzawauza 
Zomwe adali kuchita. 

160. Amene wachita chabwino 
alipidwa Zabwino khumi zofanana 
ndi icho. Ndipo amene wachita 
choipa adzalipidwa koma chonga 
icho (Popanda kuonjezera). Ndipo 
Iwo sadzaponderezedwa. 2 



%?&%$¥'* ^">' 



■la* 






%m^ 






1 Chisilamu kuti chikamthandize munthu nkofunika kuti achigwiritsire ntchito 
pamoyo wake wonse. Chisilamu chokha popanda kuchigwiritsira ntchito 
sichikwanira ndiponso sichingamtchinjirize munthu kuchilango chamoto. 
Ndipo yemwe sali Msilamu kuti Chisilamu chikamthandize nkofunika kuti 
alowe m'Chisilamu ali ndi moyo, osati pamene imfa yamufika. Ndipo nayenso 
Msilamu wochita zoipa, akalapa imfa itamufika kale kulapa kwakeko 
sikungamthandize. Koma alape pamene ali ndi moyo wangwiro. Pamenepo 
ndiye kuti Mulungu alandira kulapa kwake. Osati kulapa uku imfa akuiona ndi 
maso ake. 

2 China mwachifundo cha Mulungu pa zolengedwa zake ndiko kuti 
adzamulipira munthu patsiku la chimalidziro mosiyanitsa pakati pa chabwino 
ndi choipa. Ngati adachita chabwino chimodzi, adzamulipira mphoto ya zinthu 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



310 



A *>l 



1 fUjSfi Oj^-O 



161.Nena: "Ndithudi, ine 
Mbuye Wanga wandiongolera 
kunjira Yoongoka, kuchipembedzo 
cholingana, Chomwe ndi 
chipembedzo cha Ibrahim, Yemwe 
adali wolungama. Sadali 
Mwaophatikiza (Mulungu ndi 
mafano). 

162.Nena: "Ndithudi, Swala 
yanga, Mapemphero anga onse, 
moyo wanga, Ndi imfa yanga, 
(zonse) nza Mulungu, Mbuye 
wazolengedwa zonse: 

163. lye alibe wothandizana 
naye. Izi ndi zomwe 
ndalamulidwa, Ndipo ine ndine 
woyamba mwaogonjera." 

164.Nena: "Kodi ndifune 
mbuye wina Kusiya Mulungu, 
pomwe lye ndi Mbuye Wachinthu 
chilichonse? Ndipo Mzimu 
uliwonse siuchita choipa Koma 
ukudzichitira wokha. Mzimu 
wosenza machimo siudzasenza 
Machimo a mzimu wina. Kenako 
Kobwerera kwanu (nonse) ndi kwa 
Mbuye wanu, (Mulungu), ndipo 
Adzakuuzani zomwe mudali 
kusiyana." 

165. Ndipo lye ndi Yemwe 
wakuchitani kukhala A 









®jf»o&te6^ 






khumi zoposera pachabwino ndipo ngati adachita choipa, sadzamuonjezera 
malipiro achoipacho koma adzamulipira chofanana ndi choipacho. Tanthauzo 
lake nkuti chabwino chimodzi malipiro ake ndi zabwino khumi; pomwe choipa 
chimodzi mphoto yake ndi choipanso chimodzi. 



Surat 6. Al-An'am Juzu 8 



311 



A *>1 



*\ pUity 5jJm» 



m'lowam'malo padziko (kulowa 
M'malo mwa anzanu omwe 
adaonongeka). Ndipo wawatukula 
paulemerero (ndi Pachuma) ena a 
inu pamwamba pa ena Kuti 
akuyeseni pazomwe wakupatsani. 
(Amene apatsidwa chuma ndi 
ulemerero, Athandize amene 
sadapatsidwe. Ndipo Amene 
sadapatsidwe, apirire asalande 
Chinthu chamwini). Ndithudi, 
Mbuye Wako ngwachangu 
pokhaulitsa. Ndiponso lye 
Ngokhululuka kwabasi 
Ngwachisoni. 1 






Ndime iyi ikusonyeza kuti kukhupuka ndi ulemerero, sindizo zizindikiro 
zosonyeza kuti munthuyo ngofunika kwa Mulungu. Ndiponso kusauka ndi 
kunyozeka sizizindikiro kuti munthuyo ngosafunika kwa Mulungu kapena 
wonyozeka kwa Chauta. Koma kulemera, ulemerero, kusauka ndi 
kunyozeka.zonsezi amazipereka m'njira yamayeso. 



Surat 7. 


Al-A'raf Juzu 8 


312 


AtjA-i 


V iJljpty «jj-. 


1 


SURAT AL-A'RAF VII 





Sura iyi idavumbulutsidwa ku Makka kupatula Aya 163 
kufikira 170. Koyambirira kwa Sura iyi ikupitiriza mawu a 
m' Surat Al - Imran. Pambuyo pake yasonkhanitsa mawu 
achiyambi chakulengedwa kwa munthu. Yafotokoza nkhani ya 
kulengedwa kwa Adamu ndi Hawa, ndikutuluka kwa awiriwa 
m'munda wamtendere, kupyolera m'manong'onong'o achinyengo 
a Satana. Yafotokozanso kuti manong'onong'o onyenga a 
Satana akupitirira ku anthu kudzera kumbali ya chovala ndi 
chakudya. 

Yafotokozanso surayi kuti anthu alingalire zolengedwa za 
Mulungu kumwamba ndi pansi monga momwe zilili Sura za ku 
Makka. 

Yafotokozanso nkhani za aneneri a Mulungu monga: Nuhi, 
Hudi ndi anthu ake (Adi). Kenako nkhani ya Swaleh ndi anthu 
ake (Asamudu), omwe ankadziwika ndi mphamvu ndi chuma. 
Yakambanso nkhani ya Luti pamodzi ndi anthu ake omwe 
ankachita za uve, ndi nkhani ya Shuaibu pamodzi ndi anthu a ku 
Midiyani. Surayi yasonkhanitsa nkhani zoona zomwe zili ndi 
malango ndi maphunziro m'kati mwake. Ndipo Mulungu 
Woyera wafotokozanso nkhani ya Musa pamodzi ndi Farawo ndi 
zomwe Farawo ndi anthu ake adapeza. Surayi yamaliza pofotokoza 
za yemwe wapatsidwa chiwongoko, kenako ndikudzichotsa 
m'chiwongokocho posokonezedwa ndi Satana ndi zomwe 
zingamtsatire pakutero. Kenako yafotokoza ulaliki wachoonadi 
omwe udadza ndi Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale 
ndi iye). 




Surat7. AI-A'raf Juzu 8 



313 A *>» 



V J>\j*H\ 3jj-- 



SuratAl-A'rafVII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni. 

1. Alif-Lam-Mim-Sdd. 

2. (Iyi Qur'an ndi) Buku 
(lopatulika) Lomwe 
lavumbulutsidwa kwa iwe. 
Choncho chifuwa chako 
chisabanike Ndi ilo (poopa 
kufikitsa mawu ake Kwa anthu 
kuti angakuyese wabodza;) Kuti 
uwachenjeze Nalo (otsutsa) ndi 
kuti likhale Chikumbutso kwa 
okhulupirira (kuti Aonjezere 
chikhulupiriro chawo). 1 

3. Tsatirani zomwe 
zavumbulutsidwa kwa Inu 
kuchokera kwa Mbuye wanu, 
ndipo Musawatsatire omwe sali 
Mulungu Powayesa atetezi (anu). 
Ndi zochepa zimene 
Mumazikumbukira. 

4. Ndi midzi yambiri imene 
tidaiononga ndipo Chilango chathu 
chidaidzera Nthawi yausiku, 
kapena usana iwo Atagona tulo 
tamasana, (akupumula Monga 
momwe zinawachitikira Anthu a 
Loti ndi anthu a Shuaibu). 



*. 






O^I^JMkU- 



i c^ 



1 ^^Ti 






Wy«S7"J» 









1 Apa akumuuza Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti asaope 
kulengeza zimene Mulungu wamuululira. Asatekeseke ndi otsutsa ngakhale 
atachuluka (bwanji) chotani. Mlaliki aliyense akuuzidwanso chimodzimodzi. 
Anene choonadi kwa anthu ndipo asaope kudzudzulidwa 



Siirat 7. Al-A'raf Juzu 8 I 314 I A *>i 



V tJljP^I 3j>- 



5. Ndipo sikunali Kulira kwawo 
pamene Chinawafika chilango 
chathu koma Kunena (ndi 
kuvomereza): "Ndithudi, Ife tinali 
ochita zoipa." (Koma Kuvomereza 
kwawoko Sikunawapindulire 
kanthu). 

6. Mtheradi tidzawafunsa 
(anthu) amene Anatumiziridwa 
(Atumiki) Naonso atumikiwo 
Tidzawafunsa. 

7. Tsono tidzawauza 
mozindikira bwino-bwino 
(chilichonse chimene ankachita). 
Ndipo sitidali kutali (nawo Pamene 
ankachita zochita zawo). 

8. Ndipo sikero (yoyezera 
zochita za Anthu) tsiku limenelo 
idzakhala Yoona (yopanda 
chinyengo). Choncho, Amene 
idzalemere miyeso yake 
(Yazabwino), iwowo ndiwo 
opambana. 

9. Ndipo amene idzapepuke 
miyeso Yawo (yazinthu zawo 
zabwino), Iwo ndi amene ataya 
pachabe moyo Wawo chifukwa 
chakuzichitira Zosalungama 
zizindikiro zathu. 

10. Ndithudi tinakupatsani 
mphamvu Yokhalira padziko, 
ndipo Takupangirani m'menemo 
Zinthu zofunika pamoyo Wanu. 
Koma kuyamika Kwanu mpang'ono. 






0i 












Siirat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



315 



A frjfci 



V JMy^l ijy* 



ll.Ndithudi, tinakulengani, 
kenako Tidakukonzani 
(pokupatsani ziwalo) Ndi kunena 
kwa Angelo kuti: "Mgwadireni 
Adamu." Ndipo adamgwadira 
Kupatula Iblis, sadali mwa 
ogwada. 

12. (Mulungu) anati: "Nchiyani 
chakuletsa Kumgwadira pamene 
ndakulamula?"(Satana) anati: "Ine 
ndine wabwino Kuposa iye. Ine 
munandilenga ndi Moto koma iye 
mudamulengaNdi dongo." 

13. (Mulungu) adati: "Choncho, 
choka M'menemo ndi kutsikira 
pansi. Sikofunika kwa iwe 
kudzitama M'menemo. Tuluka, 
ndithu, iwe Ndiwe mmodzi wa 
onyozeka." 1 

14. (Satana) anati: "Ndipatseni 
Nthawi mpaka tsiku Limene 
adzaukitsidwa (Akapolo anu ku 
imfa)." 

15. (Mulungu) Adati: "Ndithudi 
iwe ndi mmodzi Wa opatsidwa 
nthawi." 

16. Iye (chifukwa cha njiru yake 
yoopsa Pa Adamu) adati: "Tsono 
chifukwa Chakuti mwandichita ine 
kukhala Wopotoka, 
ndidzawakhalira (akapolo Anu 












«ssaK(Jitsjw* 






Mulungu anamtulutsa m'nyumba ya 
chakudzitama ndi kunyoza tamulo la Mulungu. 



ulemerero Wake chifukwa 



Surat7. AI-A'raf 



Juzu 8 



316 



A t >i 



V iJljpty 6jf 



ndikuwabisalira) panjira yanu 
Yoongoka (ndi cholinga 
chowasokeretsa)". 

17. Kenako ndidzawadzera 
(mbali ya) Kutsogolo kwawo, 
m'mbuyo mwawo; Kumbali 
yakumanja kwawo ndi kumanzere 
Kwawo, mwakuti simudzapeza 
ambiri A iwo oyamika. 

18. (Mulungu) anati: "Tuluka 
m'menemo, Uli wonyozeka ndi 
wothamangitsidwa. Amene 
adzakutsata iwe mwa iwo, 
Ndithudi, (ndikamponya kumoto). 
Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannama 
ndi Inu nonse." 

19. (Kenako Mulungu adanena 
kwa Adamu) "E iwe Adamu! 
Khala ndi mkazi wako M'munda 
wa Mtendere, (sangalalani ndi 
Zomwe zili m'menemo) idyani 
Paliponse pamene mwafuna. Koma 
mtego Uwu musawuyandikire 
kuopera kuti Mungakhale m'gulu 
la odzichitira okha zoipa." 

20. Satana adayamba 
kuwanong'oneza (Zoipa) kuti 
chioneke kwa iwo Chimene 
chinabisika kwa iwo monga 
Umaliseche wawo. Ndipo (Satana) 
Adati: "Mbuye wanu sadakuletseni 
Mtengo uwu, koma pachifukwa 
chakuti Mungasanduke angelo 
awiri, kapena Kuti mungakhale 
amuyaya." 



9 ''9 *\< * '*J> 9 'i 9<9w9J£'M4. 









Q&fyvt 






Surat7. Al-A'raf Juzu 8 



317 



A *jJM 



V tJt^ty 5j>- 



21. lye adaalumbirira onse awiri 
kuti: "Ndithudi, ine ndine Mmodzi 
mwa olangiza (Ndikukufunirani 
zabwino)." 

22. Adawakopa mwachinyengo. 
Ndipo Pamene adalawa zipatso za 
mtengowo Umaliseche wawo 
udaoneka kwa iwo Nayamba 
kudziphatika Masamba (a 
mitengo) a m'mundamo. Ndipo 
Mbuye wawo adawaitana 
(Mowadzudzula nati:) "Kodi 
sindinakuletseni Mtengowu ndi 
kukuuzani kuti Satana ndi mdani 
wanu woonekeratu?" 

23. Iwo (Adamu ndi mkazi 
wake) adati: (Modzichepetsa), 
"Tadzichitira Tokha zoipa, E Mbuye 
wathu! Ngati Simutikhululukira 
ndi kuchita nafe Chifundo ndiye 
kuti tikhala mwa otaika." 

24. (Mulungu) adati: "Tsikani 
pansi uku Pali chidani pakati panu. 
Ndipo Padziko lapansi ndi pokhala 
panu Ndi kusangalala kwanu 
mpaka m'nthawi Yoikidwayo". 

25. (Mulungu) adatinso: 
"Muzikakhala moyo pamenepo, 
Ndipo muzikafa Pamenepo; ndipo 
Momwemo mudzatulutsidwa 
(Mutauka kwa akufa)." 

26. (Mulungu adati kwa ana 
onse a Adamu): E inu ana a Adam! 
Ndithu tatsitsa kwa inu Chovala 



&2ft^<i$$ ®^l 



©I 



s* 















Siirat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



318 



A *>! 



V cily^l 5jj-- 



chobisa umaliseche wanu ndi 
Chodzikongoletsera nacho. Koma 
Chovala choopa nacho Mulungu 
(Pakudziyeretsa ku zoletsedwa) 
Chimenecho ndicho chabwino 
koposa. Zimenezo ndi zizindikiro 
Za (chisomo cha) Mulungu Kuti 
iwo akumbukire. 

27. E inu ana a Adam! Satana 
Asakusokonezeni monga momwe 
Adawatulutsira makolo anu 
M'Munda wamtendere ndi 
kuwavula Onse awiri chovala 
chawo kuti Awasonyeze 
umaliseche wawo. Ndithu, iye ndi 
mtundu Wake akukuonani pomwe 
inu Simukuwaona. Ndithu, 
asatanaTawachita kukhala abwenzi 
a Osakhulupirira. 

28. Ndipo (osakhulupirira) 
akachita Chauve amanena: "(I c hi) 
tidawapeza Nacho makolo athu 
(akuchichita) Ndiponso Mulungu 
watilamula Chimenechi." Nena: 
"Ndithu Mulungu Salamula 
zonyasa. Kodi mukumunenera 
Mulungu zomwe simukuzidziwa?" 

29. Nena: "Mbuye wanga 
walamula Chilungamo; ndiponso 
(wandiuza Kuti ndikuuzeni kuti) 



*&$&$2fr4)&$g. 



? 9* 9 ifoC "9 9 9 S i 'L fify\ v 






9^' 9? 9l99 9*<**f ,ft 9»*"< 9 I 



Mulungu akutiuza kuti tivale nsalu zomwe Mulungu adatipangira kuti 
zikongoletse matupi athu. Komatu akutilamulanso kuti tivale nsalu 
zokongoletsa mitima yathu; nsalu yomwe njotsatira nayo malamulo a Mulungu 
ndi kuletsa zomwe lye waletsa; ndi kuchita zokhazo zomwe Mulungu 
walamula. Nsalu imeneyi ndi "takuwa" (kuopa Chauta). Sibwino kukongoletsa 
kunja kwa thupi kokha pomwe mumtima mwadzadza zauve. 



Surat 7. Al-A'raf Juzu 8 



319 



A ftj*-i 



V cJiy^i Sjj- 



lungamitsani Nkhope zanu (kwa 
lye) m'nthawi ya swala iliyonse, 
ndipo mpembedzeni lye yekha 
momuyeretsera chipembedzo 
Monga lye adakulengani 
pachiyambi, Momwemonso 
mudzabwerera kwa lye." 

30. Gulu Una 
waliongola,pomwe gulu Lina 
patsimikizika pa ilo kusokera 
Chifukwa chakuti iwo adasankha 
Asatana kukhala atetezi awo 
Kusiya Mulungu; ndipo akuganiza 
Kuti iwo ngoongoka. 

31. E inu ana a Adamu ! 
Tengani (valani) Zovala zanu 
zabwino pamene 
Mukukapemphera Swala iliyonse 
ndipo Idyani ndi kumwa; koma 
Musapyoze muyeso. lye 
(Mulungu) sakonda opyoza 
muyeso (Oononga). 

32. Nena: "Ndani waletsa 
zokongoletsa Za Mulungu, 
(zovala), zomwe lye (Mulungu) 
adawatulutsira akapolo ake ndi 
Zakudya zabwino?" Nena: "Zinthu 
zimenezo nzololedwa Kwa amene 
akhulupirira (Asilamu) Pamoyo 
wapadziko lapansi. (Zidzakhala) 
zawozawo tsiku la Chimaliziro. 
M'menemo ndi mom we 
Tikulongosolera aya Zathu kwa 
Anthu ozindikira." 



^&$WT>&Q 












©, 






1 Padali anthu ena omwe adali ndi chikhulupiriro choti kuvala nsanza ndi 



Surat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



320 1 A *>» 



V cil^l Sj^ 



33. Nena (kwa iwo): "Ndithu 
Mbuye wangaWaletsa zinthu 
zauve zoonekera ndi zobisika, Ndi 
machimo, ndi kuwukira 
(atsogoleri) Popanda choonadi, ndi 
kumphatikiza Mulungu ndi 
chomwe sadachitsitsire Umboni 
(wakuti chiphatikizidwe ndi lye); 
ndiponso (waletsa) kumunenera 
Mulungu zimene simukuzidziwa. l 

34. Anthu onse ali ndi nthawi 
yawo Yawo (yofera). Ndipo 
nthawi yawo Ikadza sangachedwe 
Ngakhale ola limodzi, ndiponso 
Sangaitsogolere. 

35. E inu ana a Adam! 
AkakudzeraniAtumiki ochokera 
mwainu namakuuzani 
Zivumbulutso zanga,(avomereni) 
choncho Omwe adzitchinjiriza 
kuzoletsedwa ndi kuchita 
Zabwino, sipadzakhala mantha pa 
Iwo ndiponso sadzadandaula. 

36. Ndipo amene atsutsa 
zivumbulutso Zathu 
nadzitukumula nazo, awo Ndi 
anthu akumoto adzakhala 
Mmenemo muyaya. 

37. Kodi ndani woipitsitsa 
koposa Kuposa munthu wopekera 















W&&i&<&0& 



kudya zinthu zosakoma ndiko kumuopa Mulungu. Mpaka masiku ano alipobe 

anthu oganiza motere. Ndipo nchifukwa chake Mulungu akuvumbulutsa aya 

izi kuti kutero sindiko kumuopa Mulungu. 

1 Choipa nchoipa basi. Kaya kuchichita moonekera kapena mobisa, 

nchoipabe. 



Surat7. AI-A'raf Juzu 8 



321 



A ftjJt-l 



V <3ljPty Sj^W 



bodza Mulungu kapena wotsutsa 
zivumbulutso zake? Iwo gawo 
(lachakudya Chimene) 
adawalembera liwafika (Pano 
padziko lapansi ngakhale Kuti 
ngosakhulupirira mwa Mulungu) 
Kufikira pomwe adzawadzera 
atumiki Athu (Angelo kudzatenga 
miyoyo yawo) Nawapatsadi imfa 
uku akunena: "Kodi zili kuti zija 
munkazipembedza Kusiya 
Mulungu?" Adzati: "Zatisowa". 
Ndipo adzadzichitira okha umboni 
kuti iwo adali Okana Mulungu. 

38. (Mulungu) adzati (pa tsiku 
lachiweruzo): "Lowani kumoto 
pamodzi ndi mibadwo Imene 
idamuka kale (inu musanabwere) 
Yochokera mziwanda ndi mu 
anthu. M'badwo uliwonse pamene 
uzikalowa, Udzatemberera unzake 
kufikira Pamene onse 
adzasonkhana m'menemo. 
Adzanena apambuyo kwa 
oyambirira Awo: "Mbuye wathu! 
Awa, adatisokeretsa. Apatseni 
chilango chamoto Chochuluka." 
(Mulungu) adzanena: "Aliyense 
mwa inu akhala ndi chilango 
Chochuluka; koma izi inu 
simukudziwa. 1 



9} 9 k 









Aliyense adzapeza chilango chachikulu. Ndipo awo amene adasokerezedwa: 

a) Adzapeza chilango chifukwa cholola kusokerezedwa pomwe adapatsidwa 
nzeru zowazindikiritsa zabwino ndi zoipa. 

b) Adzapeza chilango chifukwa chochita machimowo. 



Surat7. Al-A'raf Juzu 8 



322 1 A *>* v ±i\jfiH\ 5j>* 



39. Ndipo oyamba adzati kwa 
otsiriza: "Inunso mudalibe ubwino 
woposa Ife; choncho , lawani 
chilango Cha zomwe mudapeza 
(m'zochitachita Zanu)." 

40. Ndithudi, amene akutsutsa 
zivumbulutso Zathu 
nadzitukumula nazo (pakukana 
Kuzitsata), sadzatsekulidwa kwa 
iwo makomo Akumwamba, ndipo 
sadzalowa kumunda Wamtendere 
mpaka ngamira idzalowe Pa 
chibowo cha singano. Umo 
ndimomwe Timawalipirira anthu 
ochimwa. 

41. Moto wa Jahannama 
(Gahena) ndi mphasa Yawo; 
ndipo pamwamba pawo Adzakhala 
ndi (chofunda chamoto) 
Chowaphimba. Umo ndimomwe 
Tikuwalipirira anthu osalungama. 

42. Ndipo amene akhulupirira 
ndikumachita Zabwino, 
sitikakamiza munthu aliyense 
Koma chimene angachithe, awo 
ndiwo Anthu a kumunda 
wamtendere. M'menemo Iwo 
akakhala muyaya. 












Tsono amene adali kusokereza anzawo: 

a) Adzapeza chilango chifukwa chakuchita kwawo machimo. 

b) Adzapeza chilango chifukwa chakuwasokeretsa anthu omwe adawasokeretsa 

c) Adzapeza chilango chifukwa chakuyambitsa machimowo 

d) Adzapeza chilango chifukwa chowasiira anzawo odza m'mbuyo mwawo 
machimo powatsanzira iwo. 



Siirat7. Al-A'raf Juzu 8 



323 



A ftji-l 



V cjly^l dj^ 









43. Ndipo tidzachotsa 
kusakondana (komwe Kudali) 
m'mitima mwawo; (adzakhala 
Okondana ngakhale padziko 
lapansi Adali odana) uku pansi ndi 
Patsogolo pawo mitsinje 
ikuyenda; Ndipo adzanena 
(m'kuthokoza kwawo): 
"Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu, Yemwe adatitsogolera 
ku ichi (chomwe Chatidzetsera 
mtendere): Sitikadaongoka 
pakadapanda Mulungu Kutiongola. 
Atumiki a Mbuye wathu Adadza 
ndi choonadi." Ndipo 
Adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): 
"Uwu ndi Munda wa Mtendere 
umene Mwapatsidwa chifukwa 
cha zomwe Mudali kuchita". 

44. Anthu akumunda 
wamtendere Adzaitana anthu aku 
moto (adzanena Kuti): "Ndithudi 
ife tapeza zimene Mbuye wathu 
adatilonjeza kuti nzoona. Kodi 
nanunso mwapeza zomwe Mbuye 
wanu adakulonjezani kuti 
nzoona?" (Anthu akumoto) 
adzanena: "Inde;" choncho 
Wolengeza pakati pawo 
azalengeza Kuti "Matemberero a 
Mulungu Ali pa anthu ochita 
zoipa." 1 



1 Mtunda umene ukakhale pakati pa kumoto ndi kumunda wamtendere 
ngwautali kwabasi ndipo palibe angauganizire kuti uli mwakutimwakuti. Koma 
ngakhale zili chonchi, anthu a kumunda wamtendere adzatha kuyankhulana 






Siirat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



324 



A ftj*-i 



V Jl^l ojj-- 



45. "Omwe ankaletsa anthu 
kuyenda pa Njira ya Mulungu 
nafuna kuikhotetsa Njirayo (kuti 
ioneke Yokhota pamaso pa anthu), 
Omwenso sadakhulupirire za tsiku 
Lomaliza." 

46. Ndipo pakati pawo (pa 
anthu Akumunda wamtendere ndi 
akumoto) Padzakhala chotchinga. 
Ndipo Pamwamba pachikweza 
padzakhala Anthu ena (ofanana 
ntchito zawo zabwino Ndi zoyipa) 
omwe akazindikira onse (A ku 
Janna ndi kumoto), ndi Zizindikiro 
zawo. Ndipo akawaitana Anthu a 
ku Janna (kuti): "Salaamun 
Alayikum (Mtendere ukhale 
painu)": Koma asanailowe uku ali 
ndi chikhulupiriro (Kuti ailowa). 

47. Ndipo maso awo 
akakatembenuzidwa (Kuyang'ana) 
kumbali ya anthu Akumoto, 
adzanena: "Mbuye wathu 
Musatiike pamodzi ndi anthu ochita 
Zoipa. (Tikhululukireni zolakwa 
Zathu. Tilowetseni ku Janna)." 

48. Ndipo anthu aja 
apachikweza Adzaitana anthu 












m^^ss^^ 



nawo anthu akumoto. Naonso akumoto adzatha kuyankhulana nawo a 
kumunda wamtendere. Pamene wailesi za kanema (TV) zisanayambike, anthu 
amene sadali Asilamu (anthu osakhulupirira) amati mawu amenewa ngopanda 
pake. Amati zidzatheka bwanji anthu okhalirana kutali kumayankhulana ndi 
kuonana? Koma Asilamu enieni adali kukhulupirira poti wonenayo ndi 
Mulungu. Koma makono nzeru za anthu zatulukira njira zolankhulirana ndi 
munthu yemwe ali kutali, ngakhale kumuona kumene, monga pa TV, wailesi 
lamya (telefoni) ndi internet. 



Surat7. Al-A'raf Juzu 8 



325 A *>» 



V JMy^i oj^ 



(akumoto). Adzawadziwa ndi 
zizindikiro zawo, Nati: 
"Sikudakuthandizeni Kuchuluka 
kwanu kuja, ngakhale Zija mudali 
kudzitama nazo. 

49. "Kodi awa siaja 
munkawalumbirira Kuti Mulungu 
sangawaninkhe Chifundo? 
(Taonani tsopano, Auzidwa kuti): 
"Lowani ku Janna. Palibe mantha 
pa Inu 5 ndiponso simudandaula." 

50. Naonso anthu akumoto 
adzaitana A ku Janna (ndikuwauza 
kuti): "Tatipungulirani madzi 
kapena Chinthu chimene Mulungu 
wakupatsani." (Anthu a ku Janna) 
adzanena kuti:"Ndithu Mulungu 
waletsa kupereka zonse Ziwirizo 
kwa osakhulupirira". 

51. Omwe adachita 
chipembedzo chawo kukhala, 
Zinthu zopanda pake ndiponso 
Masewero; ndipo udawanyenga 
moyo Wam'dziko. Choncho, lero 
Ifenso Tiwaiwala (tiwaleka 
kumoto) monga Momwe 
adakuiwalira kukumana ndi Tsiku 
lawo ili, ndi chifukwa Chakukana 
kwawo zivumbulutso zathu. 

52.Ndithudi, tawabweretsera 
Buku lomwe Talifotokoza 
mwanzeru, lomwe ndi Chiongoko 
ndi chifundo kwa anthu Okhulupirira. 

53. Kodi chiliponso chomwe 
akudikirira Osati zotsatira zake (za 












&>'*"& 



^J&SQ&J 






Surat7. Al-A'raf Juzu 8 



326 I A*>) 



V <J\j*H\ «j>- 



Bukulo)? Ndipo tsiku lakudza 
zotsatira Zake, adzanena amene 
kale sadalilabadire: "Ha! Atumiki 
a Mbuye Wathu adadzadi ndi 
choonadi. (Tsopano tikuvomereza) 
. Kodi Tingakhale nawo ife 
aomboli oti Atiombole (kwa Mbuye 
wathu)? Kapena tingabwezedwe 
kuti tikachite (Zabwino) osati zija 
tinkachita?" Zoonadi adziononga 
okha, ndipo Zawasowa zabodza 
zomwe adali kupeka. 

54. Ndithudi, Mbuye wanu ndi 
Mulungu Yemwe adalenga 
thambo ndi nthaka M'masiku 
asanu ndi limodzi. Kenako 
adakhazikika Pampando wake 
wachifumu. Amauchita usiku kuti 
uvindikire Usana, zimatsatana 
mwamsangamsanga. Ndipo dzuwa 
ndi mwezi ndi nyenyezi 
Nzofewetsedwa, (zikuyenda 
mogonjera) ndi Lamulo Lake. 
Dziwani kuti kulenga Nkwake, 
ndiponso kulamula nkwake. 
Ndithudi, watukuka Mulungu 
Mbuye Wazolengedwa (zonse). 

55. Mpempheni Mbuye wanu 
Modzichepetsa ndi 
Mwakachetechete (mosakuwa) lye 
(Mulungu) sakonda Opyola malire. 1 



*9t>' m '\9l\4X*> 39*' 









Zopempha zathu tikamampempha Mulungu tikuuzidwa kuti tizipempha 
modzichepetsa ndi mopanda phokoso. Tisamachite phokoso pamene 
tikupempha "maduwa" monga zikuchitikira m'misikiti yambiri masiku ano 
pakuti amene tikumpemphayo sali kutali ndi ife ndipo amamva chilichonse. 



Surat7. AI-A'raf Juzu 8 



327 



Af>l 



V tJyty Sjj- 






56. Ndipo musaononge padziko 
Pambuyo popakonza. Mpempheni 
(Mulungu) mwamantha ndi 
Mwakhumbo. Ndithu, Chifundo 
cha Mulungu chili pafupi kwa 
(anthu Ake ) Ochita zabwino. 1 

57. Ndipo lye ndi Yemwe 
amatumiza mphepo kuti Ikhale 
nkhani yosangalatsa patsogolo pa 
Chifundo chake (mvula), kufikira 
Mphepoyo itasenza mitambo 
yolemera Yomwe tikuitumiza 
kudziko lakufa. Ndipo kupyolera 
mwa iyo tikutsitsa Mitundu 
yosiyanasiyana ya Zipatso. 
Momwemo ndimo Tidzawaukitsira 
akufa. (Zonsezi) nkuti Inu 
mukumbukire. 2 

58. Ndipo m'nthaka yabwino 
umatuluka mmera Wake 
(mwachangu) mwachilolezo cha 
Mbuye wake. Ndipo nthaka 
yomwe ili yoipa siitulutsa (mmera 
wake) koma Movutikira. 
M'menemo ndi momwe 
Tikuchifotokozera chivumbulutso 
Momveka kwa anthu oyamika. 3 



Chifundo cha Mulungu chimawafika anthu omwe amachitiranso chifundo 
anzawo. Ndipo amene sachitira anzawo chifundo sangapezenso chifundo cha 
Mulungu. Choncho tiyeni tilimbikire kuthandiza ofooka ndi osowa chithandizo. 
Ngati sititero ndiye kuti chifundo cha Mulungu chidzakhala kutali nafe. 

2 Mmene Mulungu amaiukitsira nthaka youma ndi madzi amvula, nameretsa 
mmera wosiyanasiyana, momwemonso ndimo adzawaukitsira akufa. Palibe 
chimene chingamkanike. 

3 Mmene ilili nthaka yopanda chonde pomeretsa mmera movutikira 
nchimodzimodzi ndi anthu oipa. Nkovuta kuwaika panjira yabwino. Koma 
tisatope ndi kutaya mtima nawo. Tiyesetsebe kuwakokera kunjira yabwino. 






Surat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



328 



A ftjJt-i 



V u>1y>Vl 5jj- 



59. Ndithudi, tidamtumiza Nuhi 
kwa anthu ake. (lye) adati: "E inu 
anthu anga! Pembedzani Mulungu. 
Inu mulibe Mulungu wina koma 
lye. Ine Ndikukuoperani chilango 
Cha tsiku lalikulu. 

60. Akuluakulu a mwa anthu 
Ake adati: "Ndithu Ife tikukuona 
kuti uli m'kusokera Koonekera 
(potiletsa izi Zomwe tidawapeza 
nazo Makolo athu)." 

61. (lye) adati: "E anthu anga! 
Palibe Kusokera mwa ine. Koma 
ine ndine Mtumiki wochokera 
kwa Mbuye Wazolengedwa! 

62. "Ndikufikitsa kwa inu 
uthenga Wa Mbuye wanga. 
Ndiponso ndikukulangizani; ndipo 
ndikudziwa zochokera Kwa 
Mulungu zomwe inu 
simukuzidziwa." 

63. "Kodi mukudabwa 
kukudzerani Ulaliki wochokera 
kwa Mbuye Wanu kudzera mwa 
munthu Wa mwa inu, (yemwe 
wadza) kuti Akuchenjezeni ndikuti 
muope (Mulungu) Ndikutinso 
muchitiridwe chifundo?" 

64. Koma adamtsutsa. Choncho, 
Tidampulumutsa iye ndi amene adali 
Naye pamodzi m'chombo. Ndipo 
Tidawamiza aja adatsutsa aya zathu. 
Ndithudi, iwo adali anthu akhungu. 1 









^'^'igiZj 






1 Nkhani ya Mneneri Nuh paliponse akuifotokoza motalikitsa. Koma m'sura iyi 
aifotokoza mwachidule. Ndipo Nuh ndi mneneri wakale kwabasi. lye adali 



Siirat 7. Al-A'raf Juzu 8 



329 



A *>i 



v sJ\j*H\ Sj^- 



65. Ndipo kwa Adi 
(tidaatumizira) M'bale wawo 
Hud. Adati: "E inu Anthu anga! 
Mpembedzeni Mulungu. Mulibe 
Mulungu wina koma lye basi. 
Kodi simungaope?" 

66. Akuluakulu a mwa anthu 
ake omwe Sadakhulupirire 
adanena: "Ife Tili kukuona kuti uli 
mu umbuli Ndipo ife 
tikukuganizira kuti ndiwe 
M'modzi wa a bodza." 

67. (lye) adati: "E inu anthu 
anga! Palibe umbuli mwa ine. 
Koma Ine ndine Mtumiki 
wochokera Kwa Mbuye 
wazolengedwa." 

68. "Ndikufikitsa kwa inu 
uthenga wa Mbuye wanga. Ndipo 
ine ndine Mlangizi wanu 
(wokufunirani zabwino), 
Wokhulupirika." 

69. Kodi mukudabwa 
pokudzerani ulaliki Kuchokera 
kwa Mbuye wanu kupyolera Mwa 
munthu wochokera mwa inu kuti 
Akuchenjezeni? Kumbukirani 
(Mtendere wa Mulungu) pamene 
Adakuikani kukhala 






®r.' -'■ 












kuwalalikira anthu a ku Iraq. Ndipo m'nthawi imeneyo pafupifupi dziko lonse 
lapansi chitukuko chidali ku Iraq monga momwe tikuwerengera m'mabuku 
ambiri yakale. Ndipo Mtumiki wamkulu yemwe adamtsogolera Nuh, ndi Idriss. 
lye adali ku Egypt (Misir). Egypt ndi Iraq ndi maiko oyamba kukhala ndi midzi 
ikuluikulu yotukuka. 



Surat7. Al-A'raf 



Juzu 8 



330 



A *>! 



V ^jt'y «j>- 



Amlowam'malo pambuyo pa 
anthu a Nuhu, Ndipo 
akuonjezerani pachilengedwe 
kukhala amisinkhu italiitali ndi 
amphamvu. Kumbukiraninso 
mtendere wa Mulungu (pothokoza) 
kuti mupambane." 

70. Iwo adati: "Kodi watidzera 
kuti Timpembedze Mulungu yekha 
ndikusiya Zomwe ankapembedza 
makolo athu? Tabwera ndi 
chimene ukutilonjezacho Ngati uli 
mmodzi mwa onena zoona." 

71. (lye) adati: "Palibe chikaiko, 
Chilango ndi mkwiyo wochokera 
kwa Mbuye wanu zakugwerani. 
Kodi Mukukangana nane pa 
zamaina (a Mafano) omwe 
mudawatcha inu ndi Makolo anu, 
pomwe Mulungu sadatsitse 
Umboni uliwonse pa milungu 
yanu Yabodzayo? Choncho, 
dikirani. Inenso ndili pamodzi 
nanu mwa odikira." 

72. Tidampulumutsa pamodzi 
ndi amene Adali naye mwa 
chifundo chathu, Ndipo tidadula 
mizu ya omwe adatsutsa 
Zivumbulutso zathu.Ndipo sadali 
okhulupirira. 

73. Kwa Asamudu tidamtumiza 
m'bale wawo, Swaleh adati: "E inu 
anthu anga! Gwadirani Mulungu; 
inu mulibe mulungu Wina koma 






a>9 



®2$&t£* 









Surat7. Al-A 4 raf 



Juzu 8 



331 * *>» 



V d>\y>H\ ojj-- 



lye basi. Chizindikiro Chochokera 
kwa Mbuye wanu chadza kwa Inu. 
Iyi ndi ngamira ya Mulungu 
monga Chisonyezo chanu 
(chizizwa chanu), Choncho, isiyeni 
izidya m'dziko la Mulungu, ndipo 
musaikhudze ndi choipa Kuopera 
kuti chingakugwereni Chilango 
chowawa kwambiri. 

74. "Ndipo kumbukirani 
(Mulungu) pamene Adakupangani 
kukhala amlowam'malo Pambuyo 
pa mtundu wa Adi. Ndipo 
Adakukhazikani pa dziko 
mwaubwino. Mukudzimangira 
nyumba zikuluzikulu Mchigwa, 
ndiponso kusema ndi Kuboola 
mapiri kukhala nyumba. Choncho 
Kumbukirani mtendere wa 
Mulungu, ndipo Musaononge 
padziko pofalitsa chisokonezo." 

75. Adanena akuluakulu omwe 
adali Odzitukumula mwa anthu 
ake kuuza Omwe 

adaponderezedwa kwa amene adali 
Okhulupirira (Mulungu) mwa iwo: 
"Kodi muli ndi chitsimikizo Kuti 
Swaleh ngotumizidwa ndi Mbuye 
Wake (wapatsidwa utumiki)? 
(Iwo) Adati: "Ndithu ife 
tikukhulupirira Zomwe watumidwa 
nazo (kuzifikitsa Kwa ife)." 

76. Omwe adadzitukumula 
Adati: "Ndithu ife Tikuzikana 
zomwe wazikhulupirirazo". 






9 "9h m $C *?'\$i 1 ml ftf^ 



>}9 












Siirat7. Al-A'raf Juzu 8 



332 



A frjJUi 



V Jljpty 5jj~» 



77. Choncho adaipha 
(adaizinga) Ngamira ndi kunyoza 
lamulo la Mbuye Wawo, nati: "E 
iwe Swaleh! Tibweletsere 
(chilango) chimene Wakhala 
ukutilonjeza ngati Ulidi mmodzi 
waotumidwa." 

78. Choncho, chivomerezi 
chidawagwira Mwadzidzidzi, 
adapezeka Ali, akufa chigwadire 
NT nyumba zawo. 

79. Tero, Swaleh adawasiya 
(nkupita Kwina kwake) uku 
akunena: "E Anthu anga! 
Ndidafikitsadi uthenga Wa Mbuye 
wanga kwa inu. Ndipo 
Ndidakuchenjezani ndi 
kukulangizani. Koma inu simufuna 
alangizi." 

80. Nayenso Luti (tidamtuma 
ndipo kumbuka) Pamene adati kwa 
anthu ake: "Kodi Mukuchita 
chonyansa chomwe 
Sadakutsogolereni aliyense 
Kuchichita mwa anthu akale 
M'zolengedwa zonse?" 

81. "Ndithu inu mukuchita 
Chisembwere ndi Amuna anzanu 
kusiya Akazi!Ndithudi, Inu ndinu 
anthu olumpha malire." 

82. Kuyankha kwa anthu ake 
sikudali kwa mtundu wina koma 
kuti: "Apirikitseni m'mudzi wanu. 
Ndithu iwowo Ndi anthu 



»< J / l» // '"'-.'Ir'i!il 9£f* 

©£aC#I 









Surat7. Al-A'raf Juzu 8 



333 



A ftji-i 



V sJ\jt*i\ dj>- 



odziyeretsa. (Choncho akhaliranji 
m'mudzi Wauve? Akakhale ndi 
anzawo Ochita zaukhondo)" 

83. Koma tidampulumutsa lye 
ndi banja Lake, kupatula mkazi 
Wake; adali m'gulu Laotsalira 
m'mbuyo (adaonongeka). 

84. Ndipo tidatsakamula Pa iwo 
chimvula (Chamiyala). Choncho, 
Taona mmene adaliri Mapeto a 
anthu oipa. 

85. Nakonso kwa anthu aku 
Madiyana, (Tidamtumiza) m'bale 
wawo Shuaib. Adati: "E inu anthu 
anga!. Gwadirani Mulungu. 
Mulibe Mulungu wina koma lye 
basi. Chitsimikizo chadza 
Kuchokera kwa Mbuye wanu. 
Choncho pimani miyeso (Yanu ya 
mbale) ndi Masikelo 

m wachi lungamo . 
Musawachepetsere anthu Zinthu 
zawo; ndipo musaononge Dziko 
pambuyo polikonza . Kutero ndi 
Kwabwino kwa inu ngati muli 
okhulupiriradi. 

86. Ndipo musamawakhalire 
anthu panjira mowabisalira ndi 
kumawaopseza Ndi kuwatsekereza 
kuyenda pa njira ya Mulungu 
amene amkhulupirira lye, Ndi 
kufuna kuikhotetsa njirayo (kuti 
Anthu asaitsate). Ndipo 
kumbukirani Adakuchulukitsani. 


















Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



334 



^ *>i 



V cJly^M 3jj- 



Taonani momwe Adalili mapeto a 
owononga. 

87. "Ndipo ngati pali gulu la 
anthu Mwa inu amene akhulupirira 
uthenga Umene ndatumidwa nawo, 
ndi gulu la Anthu limene 
silidakhulupirire, pirirani Mpaka 
Mulungu aweruze pakati Pathu. 
lye Ngwabwino poweruza Kuposa 
oweruza." 

88. A kuluakulu a omwe 
adadzikuza Mwa anthu ake, 
adanena: "Tikupirikitsa. E! Iwe 
Shuaib m'mudzi mwathu Muno 
ndi amene akhulupirira Pamodzi 
nawe, pokhapokha Mutabwerera 
kuchipembedzo Chathu." (lye) 
adati: "Kodi ngakhale Kuti 
tikuchida?" 

89. "Ngati titabwerera 
mchipembedzo chanu Pambuyo 
potipulumutsa Mulungu 
m'menemo, Ndiye kuti tampekera 
Mulungu bodza. Sikungatheke kwa 
ife kubwerera M'chipembedzo 
chimenecho pokhapokha Atafuna 
Mulungu, Mbuye wathu. Mbuye 
wathu Ngodziwa zonse. Ndipo 
kwa Mulungu yekha ndiko 
Tayadzamira. Mbuye Wathu! 
Weruzani mwachoonadi pakati 
Pathu ndi pakati pa anthu athu. Inu 
Ngabwino poweruza kuposa 
oweruza." 









^3 



si 





Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



335 



* fr>i 



V >J\je>H\ ijj~> 



90. Ndipo akuluakulu mwa 
anthu ake omwe Sadakhulupirire 
adati: "Ngati mutsatira Shuaibu 
Pamenepo ndiye kuti inu mukhala 
otayika." 

91. Choncho chivomerezi 
chidawaononga Mwadzidzidzi 
motero adapezeka akufa 
Chigwadire kunyumba zawo. 

92. Amene adamutsutsa 
Shuaibu adakhala ngati 
Sadakhalepo m'mudzimo. Amene 
adamutsutsa Shuaibu ndi omwe 
adali otayika. 

93. (Pamene nthawi 
yakuonongeka kwawo 
Idayandikira, Shuaibu adatuluka 
M'mudzimo pamodzi ndi aja 
Adakhulupirira) nawasiya oipawo 
(Kunka kutali) uku akunena, "E 
Inu anthu anga! Ndinafikitsadi 
uthenga wa Mbuye Wanga ndipo 
Ndinakuchenjezani ndiye Nchotani 
ndiwadandaulire anthu okanira 

94. Ndipo palibe pamene 
tidamtuma mneneri Aliyense 
m'mudzi uliwonse (nkumukana 
anthu A m'mudzimo) koma 
tinkawalanga eni Mudziwo ndi 
masautso ndi mavuto kuti afatse 
(Ndi kulambira Mulungu; koma 
ayi adakanika). 

95. Kenako tinasintha pamalo 
pa choipa Pobweretsapo chabwino, 



** 















&&\#&\Gm&'£ 



Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



336 



% fr>i 



V d>ly^l o^j-- 



(tidawachotsera Masautso ndi 
mavuto ngakhale sadali 
Okhulupirira) mpaka anachuluka, 
ndi Kuchulukanso chuma chawo; 
anayamba Kunena kuti: "Masautso 
ndi mavuto Adawakhudzaponso 
makolo athu. (Zoterezi 
Sizachilendo kwa ife)." Choncho 
tidawaononga Mwadzidzidzi 
asakudziwa. 

96. Chikhala kuti eni midziwo 
Adakhulupirira naopa (Mulungu 
pamene Aneneri adawadzera), 
tikadawatsekulira Madalitso 
ochokera kumwamba ndi Pansi. 
Koma adakana (ndi kutsutsa 
Aneneri) ndipo tidawaononga 
chifukwa Cha zoipa zomwe 
ankachita. l 

97. Kodi anthu a m'mizinda 
(iyo momwe Muli anthu oipa) ali 
ndi chitetezo Cholimba kuti 
chilango chathu Sichingawadzere 
usiku iwo ali mtulo? 

98. Kapena anthu a 
m'mizindayo ali ndi Chitetezo 
cholimba kuti chilango Chathu 
sichingawafike masana uku Iwo 
akusewera? 

99. Kodi akudziika pa chitetezo 
ku Chilango cha Mulungu? 
Sangadziike Pa chitetezo ku 


















1 Apa tanthauzo lake nkuti akanapeza mtendere wambiri pompano padziko 
lapansi akadakhala kuti adali olungama. 



Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



337 * *> 



V Jl^pty ojj-* 



chilango cha Mulungu Kupatula 
anthu otayika basi. 

100. Kodi sadadziwe awa omwe 
alandira Dziko molowa mmalo 
pambuyo pa Eni dzikolo (anthu 
akale) kuti Tikadafuna tikadawaika 
m'masautso Chifukwa cha 
machimo awo ndi Kuwadinda 
mitima yawo kotero iwo 
Sakadamva (kanthu)? 

101. Iyo ndi midzi (ikuluikulu) 
yomwe Tikukusimbira iwe zina 
mwa nkhani Zake. Ndithudi, 
adawadzera aneneri Awo ndi 
zizindikiro (zoonekera Poyera 
zosonyeza kuti iwo ndi atumiki A 
Mulungu). Koma sadali oti 
nkukhulupirira Pa zomwe 
adazitsutsapo kale. Umo ndi 
Mmene Mulungu amadindira ndi 
kuitseka Mitima ya osakhulupirira 
(kotero kuti Sangathandizike ndi 
malangizo a mtundu Uliwonse). 

102.Ndipo ambiri a iwo 
sitidawapeze Akukwaniritsa 
lonjezo lililonse koma Tidawapeza 
ambiri a iwo ali opandukira 
Chilamulo cha Mulungu. 

103. Pambuyo pawo 
(aneneriwo) tidamtumiza Musa 
pamodzi ndi zizindikiro zathu Kwa 
Farawo ndi nduna zake, koma 
Adazikana (zizindikirozo). 
Choncho Taona momwe adalili 
mathero aoononga 









»'**<wi 












Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



338 



* *>i 



v >J\j*H\ Sj^ 



104.Ndipo Musa adati: "E iwe 
Farawo! Ine ndine mthenga 
wochokera kwa Mbuye wa 
zolengedwa zonse. 

105. "Ndikofunika kwa ine kuti 
ndisamnenere Mulungu 
chilichonse koma choonadi Basi. 
Ndithu ndakudzerani ndi 
chizindikiro Choonekera 
kuchokera kwa Mbuye wanu. 
Choncho, aleke ndinke nawo ana a 
Israeli." 

106. (Farawo) adati: "Ngati 
Wadza ndi Chizindikiro, Bwera 
nacho (tichione), Ngati iwe ulidi 
mmodzi Wa onena zoona." 

107. Choncho adaponya ndodo 
Yake pansi. Mwadzidzidzi, 
Idasanduka njoka yooneka. 

108.Ndipo adatulutsa dzanja 
Lake pompo lidakhala Loyera, 
lowala kwa oliona. 

109. Nduna za mwa anthu a 
Farawo zidati: "Ndithu, Uyu ndi 
wamatsenga Wodziwa (kwambiri 
zamatsenga)". 

110. "Akufuna kukusamutsani 
Mdziko mwanu. Nanga 
mukuganiza zotani?" 

111. (Iwo) adati (kwa Farawo): 
"Muleke Pang'ono iye ndi mbale 
wakeyu (Usawaphe); ndipo tumiza 
osonkhanitsa M'mizinda kuti 









e,?>1 >»<?(' \Jt'1>' * 



Surat7. AI-A'raf 



Juzu 9 



339 



S *>i 



V *JijP^I 5jj^ 



akusonkhanitsire (Amatsenga onse 
akuluakulu)." 

112."Kuti akubweretsere 
Wamatsenga aliyense Wodziwa 
kwambiri." 

113. Amatsenga adadza kwa 
Farawo; Nati: "Kodi ife tipeza 
Malipiro ngati Titapambana?" 

114. (Farawo) adati: "Inde, 
Ndipo mudzakhala Mwa 
oyandikitsidwa. (Mudzakhala 
nduna zanga)." 

115. (Amatsenga) adati: "E 
iwe Musa! Kodi uyamba kuponya 
ndiwe (matsenga ako Pamaso pa 
anthu), kapena ife tikhale 
Oyambirira kuponya?" 

116. Musa adati: "Ponyani." 
Choncho Pamene adaponya 
adalodza maso a anthu 
Ndikuwaopseza. Ndipo adadza 
ndi Matsenga aakulu. 

117. Ndipo tidamzindikiritsa 
Musa ndi Chivumbulutso (Kuti): 
"ponya ndodo Yako." Pompo iyo 
Idameza zamatsengazo. 

118. Choncho, choonadi 
chidaimirira (Chidatsimikizika). 
Ndipo zidapita Pachabe zomwe 
ankachita. 

119. Choncho adagonjetsedwa 
Pamenepo, Nakhala onyozeka. 



, t£.'i4' 



®j&j£Ch'£& 









9\ m ' 9 9 /f • ' 9l 9S9C 9 if 

E /^/J/i^r^/t / < \**' %»'9 *£,* 



Sta^^tie^)^ 



Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



340 



^ *>i 



V ui^Sl 5j>- 



120.Ndipo amatsenga 
adadzigwetsa Uku akulambira 
(Mulungu). 

121. Adati: "Takhulupirira Mwa 
Mbuye wa Zolengedwa zonse." 

122. "Mbuye wa Musa Ndi 
Haaruna." 

123. Farawo adati: 
"Mwamkhulupirira Chotani iye 
ndisanakupatseni chilolezo? 
Ndithu, iyi ndi ndale yomwe 
mwaichita Mu mzindamu (inu ndi 
Musa) kuti Muwatulutsemo eni 
mzindawo. Koma Posachedwa 
mudziwa (chimene ndikuchiteni)." 

124."Ndithudi, nditseteka 
manja anu ndi Miyendo yanu 
mosinthanitsa: (kudulaDzanja 
lakudzanjadzanja ndi mwendo 
Wakumanzere, kapena dzanja la 
Kumanzere ndi mwendo 
wakudzanjadzanja). Kenako 
ndikupachikani nonsenu." 

125. (Iwo) adati: "Ifekwa 
Mbuye wathu nkobwerera". 

126. "Komatu palibe choipa 
chimene waona mwaife Kupatula 
kuti takhulupirira zizindikiro za 
Mbuye Wathu pamene zatidzera. E 
Mbuye wathu! Titsanyulireni 
chipiriro, ndipo tipatseni Imfa uku 
tili Asilamu (ogonjera Inu)." 



i> {£$$* ?>2J1 <j$5 



& &^v£jS2(gte 












&u&VV£P Vim 






Surat7. AI-A'raf 



Juzu 9 



341 



* *>i 



V Jljfrty 5jJ-rf 



127. Ndipo nduna za mwa anthu 
a Farawo Zidati (kwa Farawo): 
"Kodi umuleka Musa ndi anthu 
ake kuti abwere ndi Chisokonezo 
m'dziko, ndi kuti akusiye iwe ndi 
Milungu yako (yomwe 
adatilangiza makolo athu Kuti 
tipembedze pamodzi ndi iwe)? 
(Farawo) Adati: "Tipha ana awo 
achimuna ndikuwasiya Amoyo 
(ana awo) achikazi. Ndithudi ife pa 
Iwo tili ndi mphamvu 
zowagonjetsera." 

128. Musa adauza anthu ake: 
"Pemphani Chithandizo kwa 
Mulungu, ndipo Pilirani. Ndithu 
dzikoli ndi la Mulungu; Alipereka 
kwa amene wamfuna mwa 
Akapolo ake. Ndipo mapeto 
abwino Nga anthu olungama." 

129. (Iwo) adati: "Takhala 
tikuvutitsidwa Kale usanatidzere 
ndiponso (tsopano) Pamene 
watidzera." (Musa) adati: "Mwina 
Mbuye wanu amuononga mdani 
Wanu ndipo akulowetsani mmalo 
mwawo M'dzikoli, ndi kuti aone 
mmene Mungachitire." 

130. Ndithu, tidawakhaulitsa 
anthu A Farawo ndi chilala, 
ndikuchepekedwa Zokolola; kuti 
mwina angakumbukire. 

131. (Adali chonchi): Ubwino 
ukawadzera, Amati, "Ubwino wu 









© 



' '. *&> 









Siirat7. Al-A'raf Juzu 9 



342 



^ *>i 



v <J\j*H\ ojj^ 



nchifukwa chazochita Zathu 
zabwino." Ndipo mliri woipa 
Ukawadzera, amakankhira kwa 
Musa Ndi amene adali naye. 
(Amati iye Ndiye wadzetsa tsokalo 
chifukwa Choisambula milungu 
yawo). Dziwani Kuti tsoka lawo 
limachokera kwa Mulungu 
(chifukwa cha zochita zawo 
Zoipa). Koma ambiri a iwo 
sazindikira. 

132. Ndipo adati (kwa Musa): 
"Chisonyezo chilichonse Chimene 
ungatibweretsere kuti utilodze 
nacho (Siupindula kanthu). Ifetu 
sitikukhulupirira. " 

133. Choncho, tidawatumizira 
chigumula, (Mliri wa) dzombe, 
nsabwe, achule ndi Magazi monga 
zizindikiro Zosiyanasiyana. Koma 
adadzikuza; Ndipo adali anthu oipa. 

134.Nthawi zonse chilango 
chikawakhudza, Amati: "E iwe 
Musa! Tipemphere kwa Mbuye 
wako pazomwe adakulonjeza. 
Ngati utichotsera chilangochi, 
ndithudi Tikukhulupirira, ndipo 
tiwatumiza Pamodzi nawe ana a 
Israeli (kuti unke Nawo kumene 
ukufuna)" 

135. Koma nthawi iliyonse 
tikawachotsera Chilangocho 
kufikira nthawi yawo Yomwe iwo 
adzaifika, pompo iwo Amaswa 
lonjezo. 



•9" M} \'*94\CCt' tji <'9&1 K> *K 












Siirat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



343 * *>» 



V sJ\j*H\ 5jj- 



136. Choncho, tidawabwezera 
chilango Ndikuwamiza m'nyanja 
chifukwa Chakuti iwo adatsutsa 
zizindikiro zathu, Ndipo sadali 
ozilabadira. 

137. Ndipo tidawalowetsa 
mmalo mwa anthu Omwe adali 
kuponderezedwa kuvuma kwa 
Dziko ndi kuzambwe kwake, 
lomwe Tidaikamo madalitso 
(ambiri). Ndipo Mawu abwino a 
Mbuye wako Adakwaniritsidwa 
kwa ana a Israeli, Chifukwa cha 
kupirira kwawo (pazomwe 
Adakumana nazo). Ndipo 
tidazigumula Ndikuziononga 
zomwe Farawo ndi anthu Ake 
ankapanga ndi zomwe ankamanga. 

138. Ndipo tidawaolotsa ana a 
Israeli panyanja (Ndi kupulumuka 
kumasautso a Farawo) Nadza kwa 
anthu omwe adali kupembedza 
Mafano awo. (Iwo) adati kwa 
Musa: "E iwe Musa! Nafenso 
tipangire milungu (yamafano) 
Monga milungu yomwe ali nayo 
iwo." (Mneneri Musa) adati: 
"Ndithudi, inu ndinu Anthu 
osazindikira. 

139. "Ndithudi awa 
aonongedwa NT zomwe ali nazozi, 
Ndiponso ndizachabe Zomwe 
akhala akuchita.". 






9< 9 ' "\2X' } s' 9 4"±\9)' ' \* 

">U 9'i?Zv'/\'<' L99 &' J 9S9* 









Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



344 



^ *>i 



V (Jl^pty Qjj^ 



140. Adati: "Kodi ndikufunireni 
mulungu Wina kusiya Mulungu 
chikhalirecho lye wakuchitirani 
zabwino zoposa Pa zolengedwa 
zonse?." 

141. Ndipo kumbukirani 
pamene Tidakupulumutsani 
(m'manja) mwa anthu A Farawo 
omwe adali kukuzunzani ndi 
chilango Choyipa ndipo anali 
kupha ana anu aamuna Ndi kusiya 
ana anu aakazi. Pa ichi Padali 
mayeso aakulu ochokera kwa 
Mbuye wanu. 

142. Ndipo tidamlonjeza Musa 
masiku Makumi atatu (kuti achite 
mapemphero Kuti kenako timpatse 
Taurat). Ndipo Tidawakwaniritsa 
ndi masiku khumi; Lidakwanira 
pangano la Mbuye wake (Lopita 
kukampatsa Tauratiyo) M'masiku 
makumi anayi. Ndipo Musa adati 
kwa m'bale wake Haaruna: "Lowa 
m'malo mwanga pa 
(kuwatsogolera) Anthu angawa. 
Ndipo konza; usatsate njira Ya 
oononga." 

143. Pamene Musa adafika 
kumalo achipangano Chathucho, 
ndipo Mbuye wake namulankhula, 
(Musa) adati: "Mbuye wanga: 
Dzionetseni Kwa ine kuti 
ndikuoneni." Mulungu adati: 
"Sungathe kundiona; koma 
yang'ana Phirilo (lomwe lili 






9 ~~k\' 9 [ 9 Y ?>?i 9 i *.*A*i 






Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



345 



^ *>» 



v <J\j*H\ ojj~> 



patsogolo pako). Ngati Likhazikika 
pamalo pake (popanda kusweka), 
Ukhoza kundiona." Choncho 
Mbuye wake Pamene adadzionetsa 
kwa phirilo adalichita Kukhala 
loswekasweka ndipo Mussa 
adagwa ndi Kukomoka. Pamene 
adatsitsimuka adati: "(Ha! 
Ndikutsimikizadi kuti) Inu ndinu 
Wolemekezeka. Ndalapa kwa Inu, 
ndipo ndine woyamba mwa 
Okhulupirira (izi)". 

144. (Mulungu) adati: "E iwe 
Musa! Ndithu Ine Ndakusankha iwe 
mwa anthu onse, (Kukusankhira) 
uthenga Wanga ndi Kuyankhulana 
Nane. Choncho landira Chimene 
ndakupatsa, Ndipo khala m'modzi 
Wa anthu othokoza." 

145. Ndipo tidamlembera 
m'magome (m'masileti) 
Maphunziro aulaliki wamtundu 
uliwonse Wofotokoza chinthu 
chilichonse: "Choncho, Agwire 
mwamphamvu ndi kuwalamulira 
Anthu ako kuti awagwire 
mwaubwino wake. Posachedwapa 
ndidzakusonyezani midzi yaoipa 
Oswa malamulo athu (momwe 
idaonongekera. Ndipo 
Ndikulowetsani inu m'menemo)." 

146. Ndiwapewetsera 
kuzilingalira zizindikiro Zanga 
awo omwe akudzitukumula 
Padziko popanda choonadi, ndipo 















Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



346 



S c>i 



V J>\j*H\ 5jj- 



Akaona chizindikiro chilichonse, 
Sachikhulupirira ndipo akaona 
njira Yolungama, sakuiyetsa njira 
(sakuitsata) Koma akaona njira 
yosokera, akuiyetsa njira 
(Akuitsata). Zimenezo nchifukwa 
Chakuti iwo adatsutsa zizindikiro 
Zathu ndipo anali osazilabadira. 

147. Ndipo awo amene atsutsa 
zivumbulutso Zathu ndi kukumana 
m'tsiku lachimaliziro, Zochita 
zawo zaonongeka. Kodi 
adzalipidwa china kuposa Zomwe 
adali kuchita? 

148. Ndipo pambuyo pake 
(popita Kukalandira Taurat), anthu 
a Musa adaumba (fano la) thole 
(mwana Wa ng'ombe) ndi 
Zibangiri zawo za siliva Ndi 
golide; yemwe adali ndi Thupi ndi 
kumatuluka mawu (koma 
Wopanda moyo). Kodi sakuona 
kuti Ilo (fano lawolo) 
silikuwalankhula. Ndiponso 
silikuwaongolera njira (yabwino?) 
Koma adalipanga basi (kuti likhale 
Mulungu wawo wa fano) potero 
adali Kudzichitira okha zoipa. 

149. Pamene adazindikira 
kulakwa kwawo, (Anadandaula 
kwambiri) naona Kuti iwo asokera, 
anati: "Ngati Mbuye Wathu 
satimvera chisoni ndi 
Kutikhululukira, ndithudi, tikhala 
mwa Otaika (oonongeka)." 









Sfi 






Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



347 



^ *>i 



V uJly^l ojj- 



150. Ndipo pamene Musa 
adabwerera kwa anthu ake ali 
wokwiya, wodandaula (pomva 
Zomwe zidachitikazo), adati: 
"Umlowam'malo wanu womwe 
mudandichitira pambuyo panga, 
ngoipa zedi. Kodi 
mudalifulumirira lamulo la Mbuye 
Wanu; (mudachita zanuzanu 
musanadziwe Chimene 
angakulamulireni Mulungu wanu)? 
Ndipo adawaponya pansi 
magomewo (Momwe 
mudalembedwa malamulo a 
Chipembedzo chake). Nagwira 
mutu wa M'bale wake nkuukokera 
kwa iye. (kufuna kummenya 
chifukwa chamkwiyo umene adali 
nawo. M'bale wakey o) adati: "E 

I we mwana wa mayi anga! Ndithu, 
Anthu (awa) adandiyesa wofooka, 
Potero (sadamvere malangizo 
anga). Adatsala pang'ono kundipha. 
Choncho Usawakondweretse adani 
(ndi chilango chako) Pa ine,ndipo 
usandiike pamodzi ndi anthu oipa". 

151. (Musa) adati: "Mbuye 
wanga! Ndikhululukireni ine ndi 
m'bale wanga ndipo tilowetseni 
m'chifundo chanu. Inu ndinu 
Achifundo kuposa achifundo 
Onse." 

152. Ndithu, omwe adapanga 
(fano la ) Thole uwafika mkwiyo 
Wa Mbuye wawo ndi kunyozeka 












Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



348 



* *>t 



v ij\j**i\ Sjj- 



Pamoyo wadziko lapansi. 
M'menemo Ndi mom we 
timawalipirira Anthu opeka (zinthu 
za chipembedzo). 

153.Ndipo omwe adachita 
zoipa, kenako Nkulapa pambuyo 
pake nakhulupirira Ndithu, Mbuye 
wako pambuyo pakulapako, 
Ngokhululuka Kwabasi, 
Ngwachisoni. 

154. Pamene mkwiyo wa Musa 
udatotobwa, adatola magome aja 
omwe m'malembo Mwake mudali 
chiongoko ndi chifundo kwa omwe 
amaopa Mbuye wawo. 

155.Ndipo Musa adasankha 
anthu ake Makumi asanu ndi awiri 
(70 omwe adali amakhalidwe 
abwino) kuti akafike kumalo a 
chipangano chathu (Chimene 
tidamuuza kuti akabwere Nawo pa 
phiripo kuti akapemphe 
Chikhululuko pamachimo awo 
omwe adachitidwa ndi anzawo 
oipa). Ndipo pamene chivomerezi 
Chachikulu chidawafika (adatsala 
Pang'ono kufa). (Musa) adati: 
"Mbuye wanga! Ngati mukadafuna 
Mukadawaononga iwo ndi ine 
Kale (pamaso pa anzawo onse kuti 
adzionere okha kuti amwalira ndi 
Mphamvu za Mulungu, osati 
Pakuwapha Ine). Kodi mutiononga 
chifukwa chazochita za mbuli 
zathu? Izi Sichina koma ndi 



«S$ftcASbg 









Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



349 



^ frjA-i 



V <J\j*H\ ojj^ 



mayesero anu. Kupyolera 
M'mayeserowo mumamlekerera 
kusokera amene mwamfuna, ndi 
kumtsogolera amene Mwamfuna. 
Inu ndiye Mtetezi wathu; 
Choncho, tikhululukireni ndi 
kutimvera Chifundo. Inu ndinu 
Abwino Mwa okhululuka onse." 

156. "Ndipo tilembereni 
zabwino padziko lino lapansi ndi 
patsiku lomaliza ndithudi 
Tibwerera kwa Inu!" (Mulungu) 
Adati: "Chilango changa 
ndichifikitsa Kwa yemwe 
ndamfuna (mwa anthu oipa); 
Ndipo chifundo changa 
chakwanira Pachilichonse (pa 
abwino ndi oipa). Koma 
ndiwalembera (kuti mtendere 
Umenewu udzakhale wawowawo 
patsiku lachimaliziro). Amene 
akupewa (zoletsedwa) ndi 
Kumapereka Zakat, ndi 
kumakhulupirira Zizindikiro zathu; 

157. "Omwe akutsata Mtumiki, 
mneneri Wosatha kuwerenga ndi 
Kulemba. (Ngakhale ali choncho, 
Akuphunzitsa zophunzitsa 
Zodabwitsa); yemwe akumpeza 
Atalembedwa kwa iwo m'Buku la 
Taurat ndi Injili, akuwalamula 
Zabwino ndi kuwaletsa zoipa, Ndi 
kuwaloleza zabwino ndi 
Kuwaletsa zodetsedwa (zoipa); 
Ndi kuwatula mitolo yawo ndi 









Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



350 



<\ *j±-l 



V <J\j*V\ Sjj-, 



Magoli omwe adali paiwo 
(malamulo Ovuta kuwatsata). 
Choncho, amene Amkhulupirira 
(Muhammad {SAW})Ndi 
kumamlemekeza ndi 
kumuthangata natsata Kuunika 
(Qur'an) komwe 

kudavumbulutsidwa Pamodzi ndi 
iye, iwo ndiwo opambana." 

158.Nena: "E inu anthu! Ine 
ndine Mtumiki wa Mulungu kwa 
inu nonse. (Mulungu) yemwe ali 
nawo ufumu Wa kumwamba 
ndipansi. Palibe Wopembedzedwa 
mwa choonadi koma Iye. 
Amapatsa moyo ndi imfa. 
Choncho, Khulupirirani mwa 
Mulungu ndi Mtumiki Wake 
yemwe ndi Mneneri Wosadziwa 
kulemba ndi kuwerenga, yemwe 
Akukhulupirira Mulungu ndi 
mawu Ake. Ndipo Mtsatireni kuti 
muongoke." 

159. Ndipo mwa anthu a Musa, 
adalipo Omwe adali kutsogolera 
anzawo ku Choonadi. Ndipo ndi 
choonadicho Ankachita 
chilungamo. 

160. Ndipo tidawagawa iwo 
m'mafuko Khumi ndi awiri 
(osiyanasiyana) Monga mitundu 
ikuluikulu. Ndipo 
Tidamuvumbulutsira Musa 
pamene Anthu ake adampempha 















Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



351 



<* *>i 



V <J\j*^ djj^ 



madzi kuti: "Menya mwala ndi 
ndodo yakoyo." Ndipo mudatuluka 
akasupe khumi Ndi awiri mwakuti 
fuko lililonse Lidadziwa malo ake 
omwera. Ndipo Tidawaphimba ndi 
mthunzi wamtambo, Ndi 
kuwatumizira mana ndi 
salwa(mbalame. Tidawauza): 
"Idyani zinthu zabwinozi Zomwe 
takupatsani." Komatu sadatichitire 
Choipa (pamene adachita 
zamphulupulu), Koma 
adadzichitira okha zoipa. 

161. Ndipo akumbutse pamene 
adauzidwa: "Khalani mu Mzinda 
uwu (Baitul Makadas, umene 
takupatsani), ndipo Idyani 
m'menemo paliponse pamene 
Mwafuna, ndipo nenani (polowa 
Mumzindamo uku mutawerama): 
"Tifafanizireni machimo athu, (O! 
Inu Mbuye wathu)." Ndipo 
Lowerani pachipata (chake) 
Modzichepetsa; tikukhululukirani 
zolakwa zanu Ndipo tiwaonjezera 
Zabwino ochita zabwino. 

162. Koma aja amene 
adadzichitira okha Zoipa, mwa iwo 
adasintha mawu ena Kusiya omwe 
adauzidwa; choncho, 
Tidawatumizira chilango 
chochokera Kumwamba chifukwa 
chodzichitira Okha zoipa. 

163. Tawafunsani nkhani ya 
mudzi umene Udali m'mphepete 









&p>-^ 



*1\ 



© cy^^-^uJI 



#. 






&%Z&J\1£3\&£&Z 



Siirat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



352 



<\ *>i 



V cily^l Ojj~- 



mwa nyanja; (Anthu 
Am'mudziwo) pamene adali 
kuswa (Lamulo la) tsiku la Sabata 
(lomwe Adauzidwa kuti patsikuli 
asamachite Usodzi wa nsomba, 
koma m'malo mwake Azichita 
mapemphero okha). Nsomba Zawo 
zinkawadzera yandayanda Patsiku 
la Sabata, koma patsiku Lomwe 
silidali la Sabata sizidali 
Kuwabwerera (yandayanda). 
Motero Tidawayesa mayeso 
chifukwa chakuchimwa Kwawo. 

164.Ndipo (akumbutse ) 
pamene anthu ena Mwaiwo 
ankanena (kwa omwe amachenjeza 
Amene adaswa kupatulika kwa 
tsiku la Sabata pamene adati): 
"Pali Phindu lanji kuwachenjeza 
anthu omwe Mulungu awapha 
kapena kuwalanga Ndi chilango 
chaukali pompano Padziko 
lapansi)? (Iwo) adati: "Kuti 
Tidzakhale ndi chidandaulo kwa 
Mbuye Wathu (ponena kuti 
tidawachenjeza Koma 
sadatimvere) ndi kutinso mwina 
Angaope (Mulungu nasiya kuswa 
lamulo Lake)". 

165. Choncho, pamene 
sanalabadire zimene Anauzidwa 
ndi kuchenjezedwa, 
Tinawapulumutsa (anthu) omwe 
amaletsa Zoipa, ndipo 
tidawakhaulitsa amene 






S&^A. 












ssa^yssuiiS^ 






Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



353 



* *>» 



V J\jfiH\ *jy~> 



Ankadzichitira okhazoipa ndi 
chilango Choipa kwambiri 
chifukwa Chakunyoza kwawo. 

166. Pamene anadzikweza 
Pakusasiya zimene Analetsedwazo 
tidawauza: "Khalani anyani, 
Oyaluka (paliponse)." 

167. Ndipo (akumbutse) 
pamene Mbuye wako Analengeza 
(kuti) adzawatumizira iwo (Ayuda) 
anthu mpaka tsiku la Kiyama, 
omwe adzawazunza ndi Mazunzo 
oipa. Ndithu, Mbuye wako 
Ngofulumira kulanga. Ndipo 
palibe chikaiko, lye Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachifundo 
chambiri. 

168. Ndipo tidawalekanitsa 
pakati pawo (Ayuda), ndi 
kuwabalalitsa padziko Lonse 
mafuko osiyanasiyana, Ena mwa 
iwo abwino (olungama) Ndipo ena 
sali choncho (oipa). Tinawayesa 
mayeso a zabwino ndi Zoipa kuti 
abwerere. (Koma ayi, 
Sanabwerere). 

169. Choncho,anawatsatira 
pambuyo (Anthu abwinowo), 
otsatira atsopano Nalandira Buku 
(la Mulungu nalowa Mmalo mwa 
iwo koma popanda Kulitsata ndi 
kulilingalira). Ankatenga Zinthu 
zoletsedwa za padziko lapansi uku 
akunena: "Tidzakhululukidwa, 















Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



354 * *& 



V Jijpty *jj-- 



(Mulungu adzatikhululukira)." 
Ngati Zina zonga izo zitawapeza, 
amazitenganso. Kodi 
silidatengedwe pangano kwa iwo 
La m'Buku kuti sadzamunenera 
Mulungu Bodza koma zoona 
zokhazokha? (Nanga Akuneneranji 
kuti Mulungu adzawakhululukira 
Pomwe akupitiriza machimo?) 
Pomwe iwo Aphunzira zomwe zili 
mmenemo. Komatu nyumba ya 
chimaliziro idzawakhalira bwino 
amene akuopa (Mulungu). Nanga 
Bwanji simukuzindikira? 

170.Ndipo amene akugwirisitsa 
Buku (la Mulungu Potsata 
zophunzitsa zake) 
ndikumapemphera Swala, 
(tidzawalipira zabwino). Ndithu, 
Ife sitipititsa pachabe malipiro a 
ochita zabwino. 

171.Ndipo(akumbutse) pamene 
tidalizula phiri Ndikulinyamula 
pamwamba pawo Monga denga 
(kapena mtambo umene 
Wawavindikira) natsimikiza kuti 
Liwagwera, (tidawauza): 
"Landirani, Mwamphamvu 
malamulo amene Takupatsani, 
ndipo kumbukirani Zomwe zili 
m'menemo (pozitsata ndi 
Kuzichita); kuti inu muope." 

172, Ndipo (kumbukirani) 
pamene Mbuye wako 
Adawatulutsa ana a Adam 



txs&s^y&& 









9 "Sf9.'< 9 '\l'<'S\i\' 



Surat7. AI-A'raf 



Juzu 9 



355 



* *>i 



V Ji^SM ojj-- 



m'misana Ya atate awo ndi 
kuwachititsa umboni okha 
(Powauza kuti): "Kodi ine sindine 
Muleri Wanu?" (Iwo adati:) u Inde 
tikuikira umboni (kuti Inuyo ndiye 
Mleri wathu)." (Mulungu 
adawauza kuti): "Kuopera kuti 
mungadzanene tsiku louka Kwa 
akufa, "Ife sitidali kuzindikira 
Chipanganochi (sitidali kudziwa 
zimenezi)." 

173. Kapena mungadzati: 
"Makolo athu ndi amene 
adapembedza mafano kale,ndipo 
Ife tidali ana odza pambuyo pawo. 
(Choncho tidawatsatira pazimene 
ankachita). Kodi nanga 
mutiononga chifukwa cha zomwe 
Adachita oipa?" 

174. M'menemo ndi mom we 
tikulongosolera Mokwanira 
zivumbulutso kuti mwina Iwo 
angabwerere (kwa Mulungu). 

175. Ndipo alakatulire nkhani za 
yemwe Tidampatsa zizindikiro 
zathu Nadzichotsa m'menemo 

(m' zizindikiro), Ndipo Satana 
namtsata iye choncho, Adali 
m'gulu laosokera. 

176. Ndipo tikadafuna 
tikadamtukula Nazo (ulemerero 
wake). Koma iye Adapendekera ku 
za mdziko natsatira Zilakolako 
zake. Fanizo lake lili ngati Galu. 









'&£<&&&&&£* 









Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



356 



* *jJH 



V <Jly^l 5jj- 



Ngati utamkalipira amathawa Uku 
akutulutsa lirime lake kunja, 
Ngakhale utamsiya amatulutsabe 
kunja Lirime lake. Umo ndi 
momwe chilili Chikhalidwe cha 
anthu otsutsa zizindikiro zathu. 
Choncho asimbire nkhani izi kuti 
angalingalire. 

177. Taonani kuipa fanizo la 
anthu omwe Atsutsa zizindikiro 
zathu ndi Kudzichitira okha zoipa. 

178. Amene Mulungu 
wamuongola ndiye Woongoka. 
Ndipo amene wamulekerera 
kusokera (Chifukwa chakusatsatira 
kwake malangizo A Mulungu), 
iwo ndiwo otaika (oonongeka). 

179.Ndithudi, majini ambiri ndi 
anthu Tidawalengera kukalowa 
kumoto wa Jahannama. Mitima ali 
nayo koma Sazindikira nayo 
kanthu; ndipo maso Ali nawo 
koma sapenyera nawo (Zodabwitsa 
za Mulungu); ndipo Makutu ali 
nawo koma samvera nawo 
(Zowapindulitsa). Iwo ali ngati 
ziweto, Kapena iwo ndi osokera 
zedi kuposa Ziweto. Iwo ndi 
osalabadira. 

180. Ndipo Mulungu ali nawo 
maina abwino. Choncho,muitaneni 
ndi maina wo. Alekeni amene 
akupotoza maina Ake 
Posachedwapa alipidwa zomwe 
akhala Akuchita 















Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



357 



^ *>i 



v *J\jP*i\ *jj~* 



181. Ndipo mwa amene 
tidawalenga, alipo Anthu 
oongolera (anzawo) kuchoonadi. 
Ndipo kupyolera mchoonadicho 
Akuchita chilungamo. 

182. Ndipo amene at sutsa 
zivumbulutso Zathu, tiwalekerera 
pang'onopang'ono, Kenako 
nkuwakhaulitsa kuchokera 
Momwe iwo sakudziwa. 

183. Ndipo ndiwapatsa 
Kanthawi. Ndithu, Kukhaulitsa 
kwanga Nkokhwima. 

184. Kodi sakulingalira 
(nkuona) kuti Munthu wawoyo 
(mneneri Muhammad{SAW}) 
Alibe misala? lye sichina chake, 
Koma mchenjezi woonekera 
poyera. 

185. Kodi saona ufumu 
wakumwamba ndi Pansi, ndi 
zinthu zomwe Mulungu Adalenga? 
Mwina mwake nthawi yawo 
Yofera yayandikira. (Nanga 
Adzalingalira liti zolengedwa za 
Mulungu?) Kodi ndi nkhani iti 
Pambuyo pa iyi (Qur'an) Imene 
adzaikhulupirira? 

186. Amene Mulungu 
wamulekerera Kusokera, alibe 
muongoli. Ndipo Mulungu 
Akuwasiya akuyumbayumba 
M'kusokera kwawo. 















?■ 






Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



358 | * *>' 



V <J\y>H\ 5jj- 



187. Akukufunsa za nthawi (ya 
Kiyama) Kuti idzakhalako liti? 
Nena: "Kudziwika kwa nthawi 
yake kuli Kwa Mbuye wanga. 
Palibe amene Angaionetse poyera 
nthawi yake Koma lye. Nkovuta 
kwambiri Kumwamba ndi pansi 
(kuizindikira Nthawi yake). 
Siidzakudzerani Koma 
mwadzidzidzi." Akukufunsa ngati 
Kuti iwe udayesetsa kufufuza za 
Nthawiyo. Nena: "Kudziwika Kwa 
nthawi yake kuli kwa Mulungu. 
Koma anthu ambiri sadziwa." 

188. Nena: "Ine ndekha ndilibe 
mphamvu Yodzibweretsera 
chabwino kapena Kudzichotsera 
choipa, koma chimene Mulungu 
wafuna. Ndikadakhala kuti 
Ndikudziwa za mseri, 
ndikadadzichulukitsira Zabwino, 
ndipo choipa Sichikadandikhudza. 
Ine sindine China chake koma 
ndine mchenjezi Ndi wouza anthu 
okhulupirira nkhani zabwino." 

189. lye ndi Yemwe 
adakulengani kuchokera Mwa 
munthu mmodzi, napanga mwa iye 
Mkazi wake kuti adzikhala naye. 
Pamene adamkumbatira, adakhala 
ndi Pakati popepuka nayenda napo 
(Mosalemedwa). Koma pamene 
(pakatipo) Padalemera 
(patangotsala pang'ono kuti 
Abereke) anampempha Mulungu, 












Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



359 



^ *>i 



V cjly^t 5j^ 



Mbuye Wawo (kuti): "Ngati 
mutipatsa mwana Wabwino 
(wooneka ngati ife), ndithu 
tidzakhala mwa Othokoza 
kwambiri." 

190. Choncho, pamene 
adawapatsa mwana Wabwino 
(yemwe adapempha) adamchitira 
Mulungu anzake (mafano) 
Pachimene Adawapatsacho.Koma 
Mulungu Watukuka kuzimene 
Akumphatikiza nazozo. 

191.Kodi akumphatikiza 
(Mulungu) ndi zinthu Zomwe 
sizilenga chilichonse pomwe izo 
Zikulengedwa? (Zikupangidwa ndi 
manja awo). 

192.Ndipo sizingathe 
kuwathandiza ngakhale 
Kudzithandiza zokha 
(podzibweretsera Zabwino ndi 
kudzichotsera zoipa). 

193. Ngati (milungu 
yamafanoyo) mutaiitanira 
Kuchiongoko, siingakutsatireni 
(chifukwa chakuti Siimva kapena 
kuzindikira chilichonse). 
Nchimodzimodzi kwainu kuiitana 
kapena kukhala chete (Palibe 
chimene ingadziwe). 

194, Ndithu, amene 
mukuwapembeza kusiya Mulungu, 
ndi akapolo monga inu. (Koma Inu 
muposa iwo). Choncho aitaneni 









® 






j>$-wd 



r\' 9 ' 99 -' 









Surat7. Al-A'raf 



Juzu 9 



360 ^ >> 



V <J\j*V\ Sj^- 



ndipo Akuyankheni ngati inu 
mulidi oona (Pazimene 
mukunenazi). 

195. Kodi iwo ali nayo miyendo 
yoyendera? Kapena ali nawo 
manja ogwirira. Kapena Ali nawo 
maso openyera? Kapena ali Nawo 
makutu omverera? Nena: 
"Aitaneni Aphatikizi anuwo, ndipo 
kenako Ndichitireni chiwembu 
ndipo Musandipatse nthawi." 

196. "Ndithu Mtetezi wanga ndi 
Mulungu, Yemwe wavumbulutsa 
Buku (Hi Lopatulika). Ndipo lye 
amawateteza ochita zabwino. 

197. "Ndipo omwe 
mukuwapembedza Kusiya lye 
(Mulungu,) sangathe 
Kukupulumutsani ndiponso 
Sangathe kudzipulumutsa okha." 

198. Ngati mutawaitanira ku 
chiwongoko, Sangamve; koma 
uwaona Akukupenyetsetsa Iwe 
pomwe iwo sakuona. 

199. Gwiritsa kukhululuka (khala 
Ndi khalidwe lokhululuka); ndipo 
Lamula zabwino ndi kudzipatula Ku 
(zochita) zambuli. 

200. Ngati manong'onong'o a 
Satana Atakuvutitsa, dzitchinjirize 
ndi Mulungu. Ndithu lye 
Ngwakumva; Ngodziwa. 

201. Ndithu amene akuopa 
(Mulungu), udyerekezi Wa Satana 






®r. 



' *99\ /■»>'&[ 



\&lS*SJ>**-v\ 









Surat7. Al-A'raf Juzu 9 



361 



H >>i 



V uJly^l 5j^ 



ukawakhudza amakumbukira 
(Mulungu), nkuona (njira yotulukira 
Muudyerekezi wakewo). 

202. Koma anzawo (omwe ali 
oipa) amawalimbikitsa m'machimo, 
ndipo Kenako saleka (kupitiriza 
machimowo). 

203. Ngati siudawabweretsere 
chozizwitsa, Akunena: "Bwanji 
wosachibweretsa Pa iwe wekha? 
Nena: "Ndithudi Ndikutsatira 
zimene zikuvumbulitsidwa Kwa ine 
kuchokera kwa Mbuye wanga. 
(Sindichita chinthu mwa ine 
ndekha). Izi (aya za Qur'an) ndi 
umboni (waukulu Pazoyankhula 
zanga) wochokera kwa Mbuye 
wanu. (Izo) ndi chiongoko Ndi 
chifundo kwa anthu okhulupirira." 

204. Ndipo Qur'an 
ikamawerengedwa, Mvetserani 
(mwatcheru) ndi kukhala Chete, kuti 
muchitiridwe chifundo. 

205. Mtchule Mbuye wako mu 
mtima Mwako modzichepetsa mwa 
Mantha ndi mosakweza Mawu 
m'mawa ndi madzulo; Ndipo 
usakhale mwa osalabadila 
(Malamulo a Mulungu). 

206. Ndithu amene ali kwa 
Mbuye wako, (Angelo), 
sadzitukumula posiya 
Kumpembedza (Mbuye wawo,koma 
Iwo) amam'lemekeza ndi 
kumlambira. 



a^^itfostftSi 









Sin at 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



362 



* *>i 



A JliiSlI «jj-> 




SURAT AL-ANFAL VIII „ j£*< 



Sura ya Al Anfal idavumbulutsidwira ku Madina, iyoyi ili ndi 
Ndime 75. Mulungu wafotokoza m'sura iyi ena mwa malamulo 
a nkhondo ndi zomwe zingachititse kuti gulu lankhondo likhale 
lopambana pa nkhondo yake.Yafotokozanso malamulo a chuma 
chosiyidwa ndi adani mmene angachigawire. 

Surayi ikufotokoza za nkhondo ya Badiri mmene inachitikira 
ndi chiyambi chake. Watchulanso Mulungu m' Surayi zakuti 
Asilamu akhale okonzekera za nkhondo poopera kuti adani 
angawadzere mwadzidzidzi ndikuti adani akafuna mtendere 
Asilamu avomereze mtenderewo. Ndipo ikumaliza surayi 
ponenetsa kuti Asilamu akhale otetezana okha, osadalira 
chitetezo cha yemwe sali m'Msilamu. 




Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



363 



S *j*-i 



A JUiSll «jj-*> 



Surat Al-Anfal VIII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Akukufunsa za chuma 
cholandidwa Pankhondo (mmene 
chingagawidwire). Nena: "Chuma 
cholanda pa Nkhondo ndi cha 
Mulungu ndi Mtumiki (ndi amene 
ali olamula Kagawidwe kake); 
choncho, Muopeni Mulungu ndipo 
yanjanani Mwachibale pakati 
panu. Mverani Mulungu ndi 
Mtumiki wake, ngati Mulidi 
okhulupirira." 1 

2. Ndithu, okhulupirira, 
weniweni ndi Amene akuti 
Mulungu akatchulidwa Mitima 
yawo imadzadzidwa ndi mantha; 
Pamenenso aya zake 
zikuwerengedwa Kwa iwo 
zimawaonjezera chikhulupiriro, 
Ndipo amayadzamira kwa Mbuye 
wawo Yekha basi; (sakhulupirira 
nyanga, Ndi mizimu ya anthu 
akufa). 2 



■f.l; 



snffife 






o^l^jJt^U- 



-^ 












Nkhondo ya Chisilamu ndinkhondo yomenyera kuti chipembedzo cha 
Chisilamu chisafafanizidwe ndi anthu ochida. Osati chifukwa chofuna kupeza 
chuma. Asilamu adafunsa Mtumiki za kagawidwe kachuma cholanda 
pankhondo ndipo anauzidwa kuti chuma cha pankhondo ncha Mulungu ndi 
Mtumiki ndi amenenso angachigawe pakati pa Asilamu. 
2 Apa patchulidwa ena mwamakhalidwe a Asilamu omwe ngokwanira 
pachikhulupiriro chawo. Amene alibe makhalidwe otere, ndiye kuti chikhulupiriro 
chawo nchosakwanira ndipo patsiku la chimaliziro sichidzawapindulira zabwino. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



364 



^ *>i 



A JUity $jj~- 



3. Amenenso amaimirira 
kupemphera Napereka chimene 
tawapatsa, (Pa njira ya Mulungu, 
ndikuthandiza Ovutika). 

4. Awa (okhala ndi makhalidwe 
otere) ndi Amene ali okhulupirira 
mwachoonadi. Iwo adzapeza 
ulemerero (wapamwamba) Kwa 
Mbuye wawo, ndi chikhululuko 
Ndi zopatsidwa zaulemu. 

5. ( Chikhalidwe cha 
Okhulupirirawa mkukanganirana 
kwawo Zotolatola za pankhondo) 
chikufanana ndi (Chikhalidwe 
chawo) pamene Mbuye wako 
Adakulamula kutuluka m'nyumba 
yako (kupita Ku Badiri kukachita 
nkhondo ndi osakhulupirira) 
Mwachoonadi. Ndithu, gulu lina la 
Asilamuwo silidafune (kuchoka 
Kukakumana ndi adani). 1 

6. Akutsutsana nawe (pa 
chinthu) choona Pambuyo pakuti 
chaonekera poyera. (Kukuwaipira 
kukumana ndi adani) ngati Kuti 
akubusidwa kunka ku imfa ali 
kuona. 

7. (Kumbukirani, E inu 
okhulupirira!) Pamene Mulungu 
anakulonjezani gulu Limodzi mwa 



cuiU^ifeS^ifcWi 






^<9 9 * '&* tftm'uK"* UK" 9 












Pamene Asilamu adauzidwa kukakumana ndi Akuraishi kuti akamenyane 
nawo nkhondo, ena mwa Asilamu adachita mantha chifukwa chakuti nthawiyi idali 
yoyamba kwa iwo kuuzidwa zokamenyana ndi adani awo, poganiziranso.kuti 
Akuraishi adali akatswiri pomenya nkhondo, ndiponso adali ochuluka zedi 
kuposa iwo. Choncho Asilamu adayesera kupereka madandaulo awa ndi awa. 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 9 



365 



* *$r\ 



A JtfiSM Ojj-- 






M«(Kl 



<?), 



tag)9KjSb' 



magulu awiri kuti likhale Lanu 
(kuti mumenyane nalo). Koma Inu 
mukufuna lopanda mphamvu kuti 
Likhale lanu (kuti ndilo 
mumenyane Nalo). Koma 
Mulungu akufuna Kuchitsimikiza 
choonadi ndi mawu Ake ndi 
kudula mizu ya osakhulupirira, 
(Pomenyana ndi gulu 
lamphamvulo, Omwe ndi 
ankhondo a Chikuraishi). 

8. Kuti achitsimikizire 
Choonadi ndi kuchichotsa 
Chachabe; ngakhale Zikuwaipira 
anthu oipa. 

9. (Kumbukirani) pamene 
mudali Kupempha Mbuye wanu 
chithandizo, Ndipo anakuyankhani 
kuti: "Ndithudi, Ine 
ndikuthandizani ndi Chikwi cha 
Angelo otsatizana Potsika, 
(omenya nkhondo)." 

10. Ndipo Mulungu sadachite 
ichi koma Kuti chikhale nkhani 
yabwino (Yosangalatsa), ndi kuti 
mitima Yanu ikhazikike ndi 
chimenecho. Ndipo Palibe 
chipulumutso (chothandiza) Koma 
chimene chachokera kwa 
Mulungu, Ndithu, Mulungu 
Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. x 

1 (Ndime 10-11) Asilamu adapeza lonjezo lochoka kwa Mulungu lakuti 
panthawi yankhondo adzawatumizira Angelo, pamenepo mitima ya Asilamu 









Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



366 



^ *>i 



A JlijSll $jj~- 



11. (Kumbukirani) pamene 
anakugonetsani Tulo tomwe tidali 
mtendere wochokera Kwa lye, 
ndipo anavumbwitsa mvula painu 
Yochokera kumitambo kuti 
akuyeretseni Nayo (matupi anu) 
ndikukuchotserani 
Manong'onong'o a Satana, 
ndikuipatsa Mphamvu mitima 
yanu ndiponso Ndikulimbikitsa 
mapazi anu (Pamchenga) 

12. (Kumbukira ) pamene 
Mbuye wako Anawauza angelo 
Kuti: "Ine ndili pamodzi nanu 
(Pokulimbikitsani ndi chithandizo 
Changa). Alimbikitseni amene 
Akhulupirira, ndipo ndidzathira 
Mantha m' mitima mwa amene 
Sadakhulupirire Mulungu. 
Choncho Amenyeni m'mitu yawo, 
ndi Kuwadula zala zawo. (Zimene 
akugwirira zida) 

13. Izi ndi chifukwa chakuti iwo 
Anapikisana ndi Mulungu ndi 
Mtumiki wake (iwo podziika mbali 
Ina kusiya komwe kudali 









o 






jdakhazikika kotero kuti ena mwa iwo adadzilotera nakhala ndi Janaba. 
Choncho panafunika kuti asambe, koma madzi panalibe. Ndipo mwadzidzidzi 
mvula idawavumbwira ndipo adapeza madzi osamba ndi ena ogwira nawo 
ntchito zina. Chigwa cha Badiri chidali chamchenga wokhawokha. Ndipo 
mchenga umene udali kumbali ya Asilamu udali wosayendeka. Munthu akati 
ayende, mapazi amangozama. Tero pamene mvulayo idavumbwa, mchengawo 
udagwirana nkukhala woyendeka. Zitatero Asilamu zidawayendera bwino. 
Koma kumbali ya Amshirikina kudali matope okhaokha. Choncho sadathe 
kuyenda mwachangu. Umo ndimomwe chifundo cha Mulungu chidalili pa 
Asilamu. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



367 



* fr>i 



A JUjSM «jj-< 



Mulungu). Amene akupikisana ndi 
Mulungu ndi Mtumiki Wake, 
ndithu Mulungu ndi Wolanga 
kwambiri (amalanga Ndi chilango 
choopsa). 

14. Chimenecho ndi chilango 
(cha Mulungu E! Inu makuraishi) 
choncho Chilaweni. Ndithu 
osakhulupirira adzapeza Chilango 
chamoto. 

15. E inu amene 
mwakhulupirira! (Choonadi) 
pamene mukumana nawo 
(Munkhondo) amene 
sadakhulupirire Alikudza kwa inu 
mwaunyinji Musawatembenuzire 
misana kuthawa. 

16. Ndipo amene 
adzawatembenuzire msana 
Kuthawa patsikulo-osati 
Kutembenuka (kwa ndale) kofuna 
kumenyana Kapena kukalowa 
m'gulu (la Asilamu)- Ndiye kuti 
adziitanira mkwiyo wochokera 
Kwa Mulungu; ndipo malo ake ndi 
ku Jahannama, Pamenepo ndi 
pamalo poipa kubwererapo. 

17. Inu simudawaphe (ndi 
mphamvu zanu) Koma Mulungu 
ndi Yemwe anawapha; 
Siudawagende pamene udagenda 
koma Mulungu ndi amene 
anawagenda (Pofikitsa mchenga 
m'maso mwawo, Wachita 






©J&1IoIl& 












Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



368 



* *>i 



A Jtfity *jj~> 



zimenezi) kuti awachitire zabwino 
Asilamu powapatsa dalitso 
labwino lochokera Kwa lye. 
Ndithu, Mulungu Ngwakumva, 
Ngodziwa. ] 

18. Izi akuchitirani (pakalipano) 
Ndithudi Mulungu afooketsa ndale 
Za osakhulupirira. 

19. Ngati mwakhala mukufuna 
chiweruzo (Pogwirira nsalu 
yovindikira ka'aba kuti 
Mupambane pankhondo), 
chiweruzo Chakudzerani 
(chokomera Asilamu). Ndipo 
Ngati musiya (kuwazunza 
okhulupirira Kapena kusiya 
kunyoza Mulungu) Chikhala 
chinthu chabwino kwa inu. Koma 
ngati mubwereza (kuwaputa) 
nafenso Tidzabwereza 
(kukulangani). Gulu Lanu 
lankhondo silikuthandizani kanthu 
Ngakhale lichuluke chotani. Ndipo 
Mulungu ali pamodzi ndi 
okhulupirira. 

20. E inu amene 
mwakhulupirira! Mverani 
Mulungu ndi Mtumiki Wake, 



<^$#^<toSS$ 



9 \'&Z'?\\»SX' *C< \9>J&* 9 \ 






Pamene nkhondo idayaka moto, Mtumiki (madalitso ndi Mtendere zikhale 
naye) adatapa mchenga naufumbata m'manja mwake naupempherera. Kenako 
adaumwaza kumbali ya adani. Ndipo mchengawo udalowa m'maso mwa 
aliyense wa adaniwo. 

Pankhondoyi anthu osakhulupirira Mulungu adali ambiri kuposa Asilamu. 
Koma ngakhale zidali choncho, Asilamu adagonjetsa adaniwo kwathunthu. 
Ambiri adaphedwa, ndipo ambirinso adagwidwa monga akaidi. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



369 



* frjJH 



A JUijSfi 3jj~- 



Ndipo musamtembenukire kumbali 
pamene Inu mukumva. 1 

21. Ndipo musakhale monga aja 
achinyengo Omwe akunena: 
"Tamva (choonadi Ndipo 
tachisunga)", pomwe iwo sakumva 
(Kumva kochigonjera). 

22. Ndithu nyama zoipitsitsa 
pamaso pa Mulungu Ndi agonthi, 
abubu amene alibe nzeru, (Omwe 
ndi Amshirikina ndi anthu 
Achinyengo). 

23. Ndipo Mulungu akadadziwa 
mwa iwo (Ndikudziwa kwake 
kopanda chiyambi); Kuti muli 
ubwino (pakuwamveretsa Qur'an 
Ndi kuwazindikiritsa) 
akadawamveretsa. (Koma 
chikhalidwe chawo chili 
chamtundu umenewo) Ndipo 
ngakhale akadawamveretsa 
(Qur'an Ndikuwazindikiritsa) 
akadatembenuka M'mbuyo uku 
akunyoza (chifukwa chakugonjera 
Zilakolako zawo). 

24. E inu amene 
mwakhulupirira (choonadi)! 
Muvomereni Mulungu (pazimene 
Akukulamulani) ndiponso 
muvomereni Mtumiki wake 















1 (Ndime 20-23). Ndime izi zikufotokoza kuipa kwa yemwe wamvera ulaliki ndi 
malangizo abwino koma naunyoza, osaugwiritsa ntchito. Ndithudi, anthu 
otere ndi anthu oipitsitsa. Koma chofunika nchakuti tikamva mawu a Mulungu 
tigwiritse ntchito pamoyo wathu onse. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



370 



* ftjA-i 



A jUiSfl 3jj-*» 



pamene akukuitanirani ku chimene 
Chingakupatseni moyo (wabwino 
wa padziko Lapansi ndi tsiku 
lomaliza). Ndipo dziwani Kuti 
Mulungu amakhala pakati pa 
munthu Ndi moyo wake 
(amautembenula mmene 
Akufunira). Ndipo dziwani kuti 
kwa lye Mudzasonkhanitsidwa. ( 

25, Ndipo muope mazunzo (a 
Mulungu a Pano padziko lapansi) 
omwe sangagwere Okhawo amene 
adzichitira zoipa mwa Inu (koma 
adzawagweranso amene akusiya 
Kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti 
Mulungu Ngolanga kwambiri. 2 

26. Ndipo kumbukirani (inu 
Asilamu) Pamene mudali 
owerengeka, ochepa, Onyozeka 
m'dziko. Mumakhala moopa 
Anthu kuti angakufwambeni, koma 
Anakupatsani pamalo pabwino 
pokhala Nakulimbikitsani ndi 
chipulumutso Chake, 



©&##j®JfJfe' 






© v-v- 



&*H5Jai» 



5&5Z \f^^%% 



1 Mu aya iyi akutiuza kuti chimene Mtumiki akutiitanira nchabwino kwa anthu 
onse, kuyambira padziko lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso 
tikuuzidwa kuti Mulungu Ngokhoza chilichonse. Akhoza kuchita chilichonse pa 
akapolo Ake palibe chimene chingalephereke. Koma ngakhale zili tero, 
Mulungu akuzimvera chisoni zolengedwa Zake. 

2 Mu aya iyi anthu olungama akuwauza kuti asalekerere anthu oipa pamene 
akuchita zoipa zawo popanda kuwaletsa chifukwa chakuti, chilango 
chapadziko lapansi chikadza chimagwera oipa ndi abwino omwe, ngakhale 
kuti abwinowo adzapeza zabwino patsiku lachimaliziro. Koma zilango 
zapadziko lapansi zimakhala za onse. Nchimodzimodzinso ndi madalitso, 
akadza amakhudza anthu onse. Choncho, nkofunika kwa anthu olungama 
kuletsa anthu osalungama kuchita zoipa, ndi kuwalangiza kuchita zabwino. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



371 



S frj*-i 



A J laity Sjj-" 



Nakuninkhani zinthu zabwino kuti 
muyamike (Mulungu). 1 

27. E inu amene 
mwakhulupirira! Musachitire 
Mulungu ndi Mtumiki (Wake) 
chinyengo (Pa kutsata zimene 
mwaletsed wa) .Ndipo 
Musazichitire chinyengo zimene 
Mwakhulupirika nazo uku 
mukudziwa (Kuti kutero 
ndikulakwa). 

28. Ndipo dziwani kuti chuma 
chanu ndi ana Anu ndimayesero 
(oyesedwa ndi Mulungu Kuti aone 
mmene mungagwiritsire nazo 
Ntchito). Ndi kuti kwa Mulungu 
Kuli malipiro akulu. 

29. E inu amene 
mwakhulupirira! Ngati Muopa 
Mulungu, adzakuzindikiritsani 
Chilekanitso (cholekanitsa pakati pa 
Choonadi ndi chachabe) Ndiponso 
akufafanizirani zoipa zanu ndi 
Kukukhululukirani. Ndipo Mulungu 
ndi Mwini ubwino waukulu. 2 

30. Ndipo (kumbukira) pamene 
omwe sadakhulupirire 
Amakuchitira chiwembu kuti 
akunjate, Kapena akuphe kapena 















y 9 " 



®&j$&&m^ 



1 Anthu akakhala mumtendere nkofunika kumakumbukira zanthawi yomwe 
adali m'masautso kuti amuyamike Mulungu pamtendere umene wawapatsawo 
ndi kupewa machimo chtfukwa chakuti palibe chomwe chimachotsa mtendere 
choposa machimo ndikusamuyamika mwini mtenderewo. 

2 Munthu ngati akuopa Mulungu moona mtima, ndiye kuti Mulungu amutsekulira 
makomo amadalitso pano padziko lapansi ndi pa tsiku la chimaliziro. 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



372 



* *>i 



A JUkSM Ojj**> 



akutulutse (M'dziko lawo la 
Makka mwachipongwe). Ndipo 
amachita chiwembu, naye 
Mulungu anawononga chiwembu 
chawocho. Ndipo Mulungu 
ndiwokhoza koposa Poononga 
ziwembu (za anthu oipa). 1 

31. Ndipo (Akuraishi) 
zikawerengedwa Aya zathu kwa 
iwo amanena: "Tidazimva (izi 
kale). Tikadafuna Tikadanena 
zonga izi. Izi sikanthu Koma 
ndinthano za anthu akale 

32. Ndipo (kumbukira) pamene 
adati: "E Inu Mulungu! Ngati ichi 
(Chimene wadza nacho 
MuhammadjSAW}) Chili 
choonadi chochokera kwa Inu, 
Tivumbwitsireni mvula ya miyala 
Yochokera mlengalenga, kapena 
Mutibweretsere chilango chowawa 
Kwambiri." 









Apa pakutchulidwa ziwembu za Akuraishi zomwe adamchitira Mtumiki 
(Madalitso ndi mtendere zikhale naye) asanasamuke ku Makka. Iwo 
adasonkhana m'nyumba yochitiramo upo nayamba kukambirana zachomwe 
angachite naye Mneneri Muhammad, chimene chingamuonongeretu. Ena 
anapereka maganizo akuti akamponye m'ndende konko ku Makka popanda 
kumpatsa chakudya. Kapena ampatse chakudya chochepa kwambiri kufikira 
afe ndi njala. Ndipo ena adati koma amtseke maso ndi milomo ndi kumnjata 
goli m'manja kenako kumkweza pangamira nkukamtaya kuchipululu 
chamchenga kuti akafere konko. 

Ena amapereka ganizo loti asankhe anyamata ochokera m'mafuko amfulu kuti 
onse pamodzi akammenye ndi kumupha. Ganizoli ndi lomwe anavomerezana. 
Koma usiku omwe adapangana kuti amuphe, ndi umene Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) adasamuka kunka ku Madina. potero adalephera 
kumupha. 

2 Aya iyi ikusonyeza kuti sadali kuchifuna choonadi, chilungamo ndi zabwino 
zomwe adadza nazo Mneneri Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye). 



Surat 8. Al-Anfal 



Juzu 9 



373 



^ *>i 



A jUity ejj-» 



33. Koma Mulungu 
sangawalange pomwe Iwe uli 
nawo. Ndipo Mulungu 
Sakadawalanga pomwe (ena mwa 
Iwo) akupempha chikhululuko. 

34. (Kodi iwo Akuraishi) ali 
ndi chinthu Chanji (chabwino 
chimene) chingamuletse Mulungu 
kuwalanga? Pomwe Iwo 
Akuwatsekereza anthu kulowa mu 
Msikiti Wopatulika. Iwo 
sanayenere kukhala Ouyang'anira 
(Msikitiwo). Palibe 
angauyang'anire koma olungama, 
Koma anthu ambiri sadziwa. ] 

35. Ndipo mapemphero awo 
panyumba Yopatulikayo sadali 
kanthu, koma Kuyimba miluzi ndi 
kuombam'manja. Choncho 
(adauzidwa): "Lawani Chilango 
chifukwa chakusakhulupirira 
kwanu." 

36. Ndithu osakhulupirira 
akupereka chuma Chawo 
(pankhondo yolimbana ndi 
Asilamu) ndi cholinga choti aletse 
Anthu kuyenda pa njira ya 
Mulungu. Adzapitiriza kupereka 
chumacho Kenako chidzakhala 
chowadandaulitsa, Ndipo 
adzagonjetsedwa. Ndipo omwe 



^J^t S^** Obi (^fc Uj 















1 M'chaka chachisanu nchlmodzi (6) chakusamuka, Mtumiki (Madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) pamodzi ndi omtsatira ake ochuluka zedi adapita ku 
Makka ncholinga chokachita mapemphero a Umra. Koma Akuraishi adamuletsa 
kulowa mumzinda wa Makka podziganizira kuti iwo ndiwo oyang'anira Kaaba. 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



374 



\ • *>i 



A JliiSlI Sjj-- 



Sanakhulupirire 
adzasonkhanitsidwa ku 
Jahannama. 

37. Kuti Mulungu alekanitse 
oipa ndi abwino Ndi kuti awayike 
ena mwa oipawo pamwamba Pa 
anzawo, potero nkuwaunjika 
oipawo mulu Umodzi, kenako 
nawaponya ku Jahannama. Iwowa 
Ndi anthu otaika. 

38. Nena kwa osakhulupirira 
kuti: "Ngati asiya (Zochita zawo 
zoipa), adzakhululukidwa Zimene 
zidatsogola. Koma ngati abwereza 
(Kuwazunza Asilamu, tiwalanga) 
ndithudi njira Ya Mulungu yomwe 
idachitika kwa anthu akale 
inadutsa (Powalanga akasiya 
kutsata malamulo a Mulungu). 

39. Pitirizani kumenyana nawo 
osakhulupirira Kufikira Shirik 
hatha ndipo chipembedzo Chonse 
chikhale cha Mulungu. Ndipo 
Ngati asiya, ndithu, Mulungu 
Ngoona Zomwe akuchita. 

40. Koma ngati apitiriza 
kunyoza kwawo, Dziwani kuti 
Mulungu ndi Mtetezi wanu, 
Mtetezi wokoma mtima koposa, 
ndi Mthandizi wabwino. 

41. Ndipo dziwani kuti 
chilichonse Chimene mwapeza 
monga chuma Cholanda 
kunkhondo,chigawo chimodzi 



\9}9)'« 9 iS?, '<* 9£\4,9fi< 



ft. • 9 . • 1%" << \, * 9 J 9\\£' 
)9 "&LI '9. ' 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



375 



\ * *>i 



A JUL»S?t tjj~> 



Mwa zigawo zisanu ndi cha 
Mulungu Ndi Mtumiki, ndi a 
chibale(a Mtumiki), Amasiye, 
masikini ndi munthu wapaulendo 
(Amene asowedwa choyendera 
paulendo. Tsatilani malamulowa) 
ngatidi Mwakhulupirira Mulungu 
(mwachoonadi) Ndi chimene 
tachivumbulutsa kwa kapolo 
Wathu pa tsiku lachilekanitso 
(Lolekanitsa pakati Pachoona ndi 
chabodza), tsiku Limene magulu 
awiri adakumana (Tsiku la 
nkhondo ya Badiri, gulu La 
nkhondo la Asilamu ndi gulu La 
nkhondo la osakhulupirira 
(akafiri). Ndipo Mulungu 
Ngokhoza kuchita Chilichonse. 

42. (Kumbukirani) pamene 
mudali mbali Yachigwa 
yoyandikira (Mzinda wa Madina) 
pomwe iwo (ankhondo a 
Chikuraishi) adali mbali yakutali 
Yatsidya lina (la chigwacho) 
pomwe Aulendo amalonda adali 
chakumunsi Kwanu. Ngati 
mukadapangana nthawi 
Yokumanirana (kuti mukumane 
nthawi Yakutiyakuti), 
mukadasiyana posunga 
Chipangano (chifukwa chakuopa 
Kuchuluka kwa adani anuwo). 
Koma (Mwakumana 
mosayembekezera ndi Ankhondo 
aadaniwo) kuti Mulungu 









Surat 8. AI-Anfal Juzu 10 



376 y * *>» 



A jUity ojj-* 



Akwaniritse chinthu chomwe 
nchofunika Kuti chichitike kuti 
awonongeke amene Waonongeka 
(posankha kusakhulupirira). Ndi 
umboni woonekera (umene 
adaukana Kuutsata). ndi kuti 
akhale ndi moyo Amene wakhala 
ndi moyo (amene watsata Njira ya 
Chisilamu) ndi umboninso 
Woonekera. Ndithudi, Mulungu 
Ngwakumva zonse, Ngodziwa 
kwambiri. 1 



1 M'ndime iyi mwatchulidwa gulu lankhondo la Asilamu ndi gulu lankhondo la 
Akuraishi ndi aulendo a chuma chamalonda a Akuraishi. Akuraishi adavutitsa 
Asilamu mu Mzinda wa Makka m'nyengo yazaka khumi ndi zitatu powalanda 
zinthu zawo ndi kuwamenya ndi kuwapha kumene. Pambuyo pake Asilamu 
adathawira ku Madina nkusiya chuma chawo chonse ku Makka. Chumacho 
chidatengedwa ndi anthu osakhulupirira Mulungu a Chikuraishi. Ndipo 
kuonjezera pazimenezi Akafiri (Akuraishi) adali kudza ku Madina usiku 
kudzaononga zinthu zambiri, pambuyo pake nkuthawa. Ndipo mwa zomwe 
adachita ndi monga kutentha nyumba ndi ziweto. Ankachitanso zifwamba 
zambiri. 

Patapita zaka khumi ndi zisanu, Asilamu akuvutitsidwabe, Mulungu 
adawapatsa chilolezo kuti amenyane ndi Akafiriwo monga momwe iwo adali 
kuwamenyera. Ndiponso kuti awalande chilichonse chimene Asilamu 
angathe kulanda kuti abweze zinthu zawo zomwe adawalanda. Choncho 
Mtumiki (Madalitso ndi Mtendere zikhale naye) adamva kuti pali ulendo wa 
Akuraishi umene wanyamula chuma chambiri ndipo udzadutsa pafupi ndi 
mzinda wa Madina. Tero, adawakhwirizira omtsatira ake (Maswahaba) kuti 
apite pamodzi naye nkukauthira nkhondo uiendowo, nkuulanda chumacho. 
Choncho anthu adamtsata okwana mazana atatu popanda kutenga zida 
zaukali zankhondo poti sadalinge kukamenya nkhondo yeniyeni koma 
adalinga kukalanda chumacho basi, chomwe chidali m'manja mwa anthu 
ochepa apaulendo; ndipo sadalinge kukawapha. Koma wotsogolera ulendo 
wamalondawo, mwamwayi adamva kuti Mtumiki ndi omtsatira ake 
akumufunafuna kuti amulande chumacho. Pompo adasintha njira natsata njira 
ina yomwe siinkayendedwa kuti asakumane ndi Mtumiki. 
Ndipo anatuma mthenga ku Makka kuti akawauze anthu am'Makka kuti iwo 
anthu amalonda athiridwa nkhondo. Akuraishi ku Makka atamva nkhani iyi, 
adasangalala. Adaona kuti apeza mwayi womumaliziratu Mtumiki Muhammad 
(SAW) ndi omtsatira ake. Choncho adatuluka atakonzeka bwinobwino 
zankhondo. Osati momwe Mtumiki ndi omtsatira ake adakonzekera. 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



377 I > • >>» 



A JUj^i 5jj^ 



43. (Kumbukira) pamene 
Mulungu adakuonetsa Iwo 
kumaloto kwako kuti ngochepa 
(Pachiwerengero chawo potero 
udalimba Mtima zakukumana 
nawo) Akanakuonetsa Iwo kuti 
ngambiri pachiwerengero chawo; 
Inu (Asilamu) mukadachita 
mantha (mukanataya Mtima) ndipo 
mukanakangana pachinthucho. 
(Ena akanafuna kumenyana nawo 
pamene ena Akanakana), koma 
Mulungu anakutetezani 
(Kuzimenezo). Ndithu, lye 
Ngodziwa kwambiri Za m'mitima. 

44. Ndipo (kumbukirani) 
pamene anakuonetsani Iwo 
m'maso mwanu, pamene 
munakumana Nawo kuti Iwo ndi 
ochepa, (owerengeka, kuti 
Mukhale ndi chidwi chomenyana 
nawo), ndiponso Anakuchepetsani 
kwambiri m'maso mwawo (Kuti 
iwo aone kuti nkosafunika 
kukonzekera Kwambiri chifukwa 









Mtumiki ndi omtsatira ake sadadziwe kuti aulendo amene iwo adali 
kuwadikirira awadutsa kale, ndi kuti gulu lalikulu lankhondo la Akuraishi 
likuwadzera kudzawathira nkhondo, ndipo lafika kale pafupi nawo Adadziwa 
za nkhaniyo pomwe iwo (Mtumiki ndi gulu lake) adali kutali ndi mzinda wawo 
wa Madina. Ndipo nkhaniyi itadziwika kwa omtsatira ake, padabuka 
mkangano pakati pawo. Ena adali ndi maganizo akuti alithawe gulu lankhondo 
la Akuraishiwo, nkupitiriza kutsatira gulu lamalonda lija, pakuti adali ndi 
chitsimikizo chonse kuti akawagonjetsa amalondawo. Koma gulu lankhondo la 
Akuraishi adalibe nalo chiyembekezo choligonjetsa naona kuti sikwabwino 
kudziika okha pachionongeko. Koma mwamwayi adakumana nalo gulu 
lankhondo la Akuraishi mosayembekezera pomwe aulendo wa malonda aja 
adali kutali nawo. 
Tero ili ndilo tanthauzo la aya ya 42. 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



378 



\ • *>i 



A JUj^M 5jj-- 



chakuchepa kwa Omenyana 
nawowo) kuti Mulungu 
Akwaniritse chimene adalamula 
kuchitika. Kwa Mulungu Yekha 
ndiko kobwerera zinthu zonse. 

45. E inu amene 
mwakhulupirira! Pamene 
Mukumana ndi gulu (la 
osakhulupirira), Mulimbe mtima, 
ndipo tamandani Mulungu 
Kwambiri kuti mupambane. 

46. Ndipo mumvereni Mulungu 
ndi Mtumiki Wake, musakangane 
(kuopera kuti) Mungachite mantha 
(ndi kutaya Mtima) Ndikuchoka 
mphamvu zanu. Koma Pitirizani 
kupirira. Ndithudi, Mulungu Ali 
pamodzi ndi anthu opirira. 

47. Ndipo musakhale ngati 
anthu amene anatuluka M'nyumba 
zawo modzikweza ndi 
Modzionetsera kwa anthu, 
ndikuwaletsa Anthu kuyenda 
panjira ya Mulungu. Koma 
Mulungu ndi Wodziwa kwambiri 
Zimene akuchita. 

48. Ndipo (kumbukira) pamene 
Satana Adawakometsera zochita 
zawo zoipa (Aja osakhulupirira) 
nati: "Lero Palibe aliyense mwa 
anthu amene Angakugonjetseni, 
ndipo ine ndine Mtetezi wanu". 
Koma pamene magulu Awiri 
ankhondo anaonana (anakumana 












Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



379 



S * *>i 



A JUi^l bjj~* 



Pamaso ndi pamaso) Satana 
anabwerera Pambuyo (kuthawa) 
nati: "Ine Ndikudzipatula mwa inu. 
Ndithu, ine Ndikuona zimene inu 
simukuziona.Ndithu ine ndikuopa 
Mulungu." Ndipo Mulungu 
Ngwaukali polanga. 

49. (Kumbukirani) pamene 
achiphamaso Ndi amene ali ndi 
matenda M'mitima mwawo 
amanena: "Anthu awa 
Chipembedzo chawo (cha 
chisilamu) Chawanyenga." 
Komatu amene akuyadzamira Kwa 
Mulungu ndithudi Mulungu 
Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru Zakuya. 

50. Ndipo ukadaona angelo 
pamene akuchotsa Miyoyo ya 
anthu amene sadakhulupirire (Pa 
imfa yawo) uku akumenya 
kunkhope Zawo ndi kumisana 
yawo (uku akunena) "Lawani 
chilango chamoto". 

51. "Izo ndi chifukwa cha 
(machimo) Amene manja anu 
anawatsogoza, Ndipo Mulungu sali 
opondereza Akapolo Ake." 1 






a<^;£Wa#u 






-T "\\ ' \ K ' \ 92 * '*' 









1 Mizjmu ya osakhulupirira ikamachotsedwa, imachotsedwa mwamasautso 
kwambiri. Koma amene ali pafupi ndi wakufayo saona zimenezi pakuti ife 
sititha kuiona mizimu ndi zonse zokhudzana ndi mizimu. Ife timangoona thupi 
lawakufayo poliona thupilo likuzunzika.Kuzunzika kwa mzimu sindiko kuzunzika 
kwathupi. Choncho kuzunzika komwe kukunenedwa apa nkuzunzika kwa 
mzimu komwe kumaapeza anthu osakhulupirira. Komatu masautso athupi 
amene amawapeza anthu ena panthawi yaimfa pophuphaphupha, sasonyeza 
kusalungama kwa munthuyo. Koma amasonyeza mphamvu zomwe zidali 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



380 



\ • ftjA-i 



A jUity ojj-* 



52. (Khalidwe lawo awa lili ) 
ngati khalidwe la Anthu a Farawo 
ndi omwe adalipo Patsogolo pawo. 
Anazikana aya Za Mulungu, 
choncho Mulungu Anawalanga 
chifukwa cha machimo A wo. 
Ndithudi Mulungu 
Ngwamphamvu, Wolanga moopsa. 

53. Izo, (posawadzera miriri 
yotere) Nchifukwa chakuti 
Mulungu sasintha Chisomo chake 
chimene wachipereka Kwa anthu 
mpaka anthuwo asinthe Okha 
zomwe zili m'mitima mwawo, 
(Posiya kuthokoza Mulungu 
nayamba Kuyenda m'njira 
zolakwira Mulungu). Ndithu 
Mulungu Ngwakumva Ngodziwa 
chilichonse. 

54. (Khalidwe lawo lili) ngati 
khalidwe La anthu a Farawo ndi 
omwe adalipo Patsogolo pawo. 
Adakana Aya za Mbuye wawo. 
Choncho, tidawaononga Chifukwa 
cha machimo awo, ndipo 
Tidawamiza anthu a Farawo. 
Ndipo Onse adali ochita zoipa. 

55. Ndithu, nyama zoipitsitsa 
kwa Mulungu ndi Amene 
sadakhulupirire (Amamkana 















m'thupi mwamunthuyo. Sizikhudzana ndi kulungama kwake ndi kusalungama 
kwake. Mungawaone anthu oipa akufa ndi imfa yodekha pomwe amene adali 
abwino akufa ndi imfa yophuphaphupha ndikudzimenyamenya. Choncho 
kuphuphaphupha kumeneko nkwathupi chifukwa chokhala ndi mphamvu, 
Choncho tisadodome pomwe tiona munthu wabwino akuphuphaphupha. 



Siirat 8. Al-Anfal Juzu 10 



381 



> * tjtr\ 



A JUi/sll 3j^» 



Mulungu ngakhale choonadi 
Akuchidziwa bwinobwino), 
choncho Iwo sakhulupirira 

56. Omwe unapangana nawo 
chipangano Kenako naaswa 
chipangano chawo Panthawi 
iliyonse (imene mwapangana) 
Ndiponso iwo saopa Mulungu. 

57. Choncho, ngati uwapeza 
kunkhondo, (Menyana nawo), 
uwabalalitse (kuti Likhale 
phunziro kwa) amene ali Pambuyo 
pawo kuti iwo azindikire. 

58. Ngati uopa kusakhulupirika 
kwa Anthu (omwe unapangana 
nawo Chipangano), atayire 
(chipangano Chawocho), 
mwachilungamo; Ndithu Mulungu 
Sakonda (anthu) osakhulupirika. 

59. Ndipo (anthu) amene 
sadakhulupirire Asaganize kuti 
ampitirira (Mulungu Kotero kuti 
sachita kanthu ndi iwo) Ai, iwo 
sangamulepheretse Mulungu 
(Chimene akufuna kuchita pa iwo). 

60. Ndipo akonzekereni mmene 
mungathere (Zomenyera 
nkhondo) ndi mphamvu zanu 
(Zonse), ndiponso poikiratu 
mahatchi odikira Nkhondo kuti 
muwaopseze nazo adani A 
Mulungu ndi adani anu (amene 
Mukuwadziwa) ndiponso (ndi ) 
Ena omwe (inu) simukuwadziwa. 


















Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



382 



> • *j*-1 



A Jlflity 0jj~* 



Koma Mulungu akuwadziwa. 
Ndipo Chilichonse mungapereke 
pa njira Ya Mulungu 
chidzalipidwa kwa inu Modzadza 
Ndipo simuzaponderezedwa. 

61. Ndipo ngati (awo adani) 
apendekera Kumbali yokhalirana 
mwa mtendere, Nawenso 
pendekera (kumbaliyo) Ukatero 
yadzamira kwa Mulungu. Ndithudi 
lye Ngwakumva, Ngodziwa. 

62. Ngati afuna kukunyenga 
pachimvanochi, Ndithudi, 
Mulungu akukwanira kwa Iwe 
(kukuteteza). lye ndi Yemwe 
anakuthangata Ndi chipulumutso 
chake ndi Okhulupirira. 

63. Ndipo (Mulungu) 
analuzanitsa pakati Pamitima yawo 
(poika chikondi pakati Pawo). 
Ngati ukanapereka zonse za 
M'dziko lapansi (ncholinga choti 
uwaluzanitse Mitima yawo mwa 
iwe wekha) sukadatha Kuluzanitsa 
pakati pa mitima yawo. Koma 
Mulungu adaluzanitsa pakati 
Pawo. Ndithu, lye Ngwamphamvu 
Zoposa Ngwanzeru zakuya. 

64. E iwe Mneneri ! Mulungu 
Akukwanira kwa iwe kukuteteza 
pamodzi Ndi amene akutsata (iwe) 
mwa Okhulupirira. 

65. E iwe Mneneri! Alimbikitse 
okhulupirira Kupita kunkhondo. 












b J$tf<m#6W 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



383 



\ * *>i 



A Jl&Sh *jj~* 



Ngati Mwa inu muli anthu 
Makumi awiri olimba Mtima 
(ndiye kuti) adzawagonjetsa 
Mazana awiri (200) (a mwa anthu 
Osakhulupirira). Ngati mwa inu 
muli anthu Zana limodzi (100) 
olimba mtima (Ndiye kuti) 
adzagonjetsa chikwi Chimodzi 
(1,000) cha anthu omwe 
Sadakhulupirire, chifukwa chakuti 
Iwo ndi anthu osazindikira. 

66. Tsopano Mulungu 
wakupeputsirani (Lamulo 
lovutali), ndipo wadziwa kuti muli 
Kufooka mwa inu. Choncho ngati 
mwa Inu muli anthu zana limodzi 
olimba Mtima adzagonjetsa 
mazana awiri. Ngati alipo mwa inu 
chikwi chimodzi, Adzagonjetsa 
zikwi ziwiri, mwachilolezo Cha 
Mulungu. Mulungu ali Pamodzi 
ndi opirira. 

67. Sichoyenera kwa Mneneri 
kukhala ndi Akayidi mpaka 
amenye nkhondo (Kwambiri) ndi 
kugonjetseratu maiko Molimba 
(ndi pamene atha kukhala Ndi 
akayidi). Mukufuna zinthu za 
M'dziko pomwe Mulungu akufuna 
(Mupeze mphoto ya) tsiku 
lomaliza Ndipo Mulungu 
Ngwamphamvu zoposa 
Ngwanzeru zakuya. 

68. Pakadapanda lamulo la 
Mulungu limene Linatsogolera 















^s&^i<S3$i 



Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



384 



\ • *>i 



A jUi^l 5jj-* 



kale, chilango Chachikulu 
chikanakugwerani, Chifukwa cha 
zimene munatenga (ku-Nkhondo 
ya Badri). 

69. Tsopano idyani chuma 
chimene mwalanda Pankhondo 
(chomwe chili) chololedwa, 
chabwino, Ndipo pitirizani kuopa 
Mulungu. Ndithu, Mulungu 
Ngokhululuka, Ngwachisoni. 

70. E iwe Mneneri (SAW) !Uza 
akaidi apankhondo Amene ali 
m'manja mwanu kuti ngati 
Mulungu aona chabwino 
chilichonse M'mitima mwanu, 
adzakupatsani Zoposa zimene 
mwalandidwa ndipo 
Adzakukhululukirani; Mulungu 
Ngokhululuka Ngwachisoni. 

71. Ngati akufuna kukuchitirani 
chinyengo (Chinyengo chawo 
sichiphula kanthu Pa iwe), ndithu 
anamuchitirapo kale Mulungu 
chinyengo (chifukwa 
Chakusakhulupirira kwawo). 
Choncho Anakupatsa mphamvu 
zowagonjetsera I wo. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa, Ngwanzeru 
zakuya. 

72. Ndithu anthu amene 
anakhulupirira nasamuka Kwawo 
ndi kumenyana pa njira ya 
Mulungu ndi chuma chawo ndi 
moyo Wawo; ndiponso amene 



^^^^V^ 















Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



385 I > • *>> 



A JtfiSlI ijj**> 



anawalandira (iwo) Ndikuwapatsa 
malo ndikuwathandiza, Awa ndi 
abale otchinjirizana Wina ndi 
mnzake. Ndipo anthu amene 
Akhulupirira koma nasiya 
kusamuka (Kudza ku Madina), 
palibe udindo Pa inu wakuwateteza 
kufikira nawonso Atasamuka 
(kudza ku Madina). Ngati 
Atakupemphani chithandizo 
chachipembedzo Athandizeni, 
kupatula (akaputana Ndi anthu) 
amene pakati panu ndi iwo Pali 
chipangano, (pamenepo 
musawathandize Pomenyana ndi 
osakhulupirirawo Omwe muli 
nawo ndi chipangano). Ndipo 
Mulungu Ngowoona zomwe 
muchita. 

73. Ndipo anthu amene 
sadakhulupirire (Mulungu) 
amatetezana okha Ndikukhala 
abwenzi pakati pawo. Ngati 
nanunso simuchita izi, Padzakhala 
chisokonezo m'dziko ndi 
chionongeko chachikulu. 

74. Amene akhulupirira 
nasamuka, namenya Nkhondo 
panjira ya Mulungu (Pamodzi 
nanu),ndiponso amene 
Anawalandira (osamukawo) 
Nawapatsa malo ndikuwathandiza, 
iwo Ndi omwe ali okhulupirira 
Mwachoonadi. iwo adzapeza 
chikhululuko ndi Zopatsidwa 
zaulemu. 















%,'J* 9 * 



<&m 






Surat 8. Al-Anfal Juzu 10 



386 



> • *j*-l 



A JbiiSM djj~> 



75. Ndipo aja akhulupirira 
pambuyo pa "Amuhajirina" ndi 
"Answari," nawonso Nasamukira; 
(ku Madina kukakhala pamodzi 
ndi Mtumiki ndi Asilamu anzawo), 
namenyanso Nkhondo pamodzi 
nanu, iwo ndi amene ali Mwainu. 
Koma achibale chakubadwana, 
ndi Amene ali oyenera 
(kulowerana mmalo pachuma. 
Zimenezo nzomwe zili) m'Buku la 
Mulungu. Ndithudi, Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 



& 







Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



387 > • *>» * *j=J» *jJ~> 




SURAT AT-TAUBAH IX 




Surat Tauba idavumbulutsidwa ku Madina m'chaka cha 9 cha 
kusamuka. Ndipo Ali, mwana wa Abu Twalib adaitenga Surayi 
kunka nayo ku Haji komwe kudali Asilamu. Ndipo adawerenga. 
Mmenemo nkuti Abubakar Swidiki ndiye adali mtsogoleri 
woyanga'nira mapemphero a Haji. 

Surayi ili ndi aya (ndime)129. Ndipo yayamba nkufotokoza 
za kudzipatula kwa Mulungu ku Amshirikina. Pachifukwa ichi 
ikutchedwanso Surat Bara'at (kudzipatula). Ndipo kenako 
yafotokoza za miyezi yopatulika ndi mapangano a Amshirikina, 
kuti adali oyenera kuwakwaniritsa ngati iwo eni sadawaswe. 
Ndipo woswa pangano ngoyenera kuthiridwa nkhondo. 

Surayi yafotokoza kuti mutu wodziyandikitsa kwa Mulungu 
ndiko kumkhulupirira lye. Chikhulupiriro sichingakhale 
chokwanira pokhapokha okhulupirira akonde kwambiri 
Mulungu ndi Mtumiki wake kuposa china chilichose. Mulungu 
wafotokozanso kuti kunyadira mphamvu kumalepheretsa 
kupambana pankhondo, monga momwe zidawachitikira 
Asilamu pankhondo ya Hunain. Ndipo m'Sura iyi, Amshirikina 
aletsedwa kulowa mu Msikiti wopatulika umene uli mu Mzinda 
wa Makka; chifukwa iwo ndi nyasi. Msurayi mulinso lamulo 
lomenyana nawo nkhondo Ayuda ndi Akhristu kufikira 
atapereka msonkho. Ndipo msurayi afotokozanso za 
chiwerengero cha miyezi yopatulika ndi kuti nkhondo ikabuka, 
nkofunika kwa Asilamu onse kupita kunkhondo. 

Msurayi afotokozanso makhalidwe a Asilamu ena omwe 
Chisilamu chawo chidali chachiphamaso; akauzidwa zopita 
kunkhondo adali kukana ndipo adalinso kulimbikitsa anzawo 
kuti asapiteko. 

Msuramu mulinso lamulo lakuti Munafiku akamwalira, 
Mtumiki asampempherere. Ndipo Surayi yafotokoza za 
chikhalidwe cha anthu kumbali ya chikhulupiriro ndi za msikiti 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



388 



\ * *>i 



S 4*f&\ 3jj-o 



womwe Amunafikina adamanga n'cholinga choti awagawe 
Asilamu pagulu lawo. Kenako Mulungu wafotokozanso za 
makhalidwe a anthu okhulupirira Chauta omwe ali oona 
pachikhulupiriro chawo, ndi kulandira kulapa kwa anthu omwe 
adatsalira mu Mzinda wa Madina Mtumiki atapita kunkhondo. 

Surayi yatsiriza nkunenetsa kuti Mulungu adasankha 
Muhammad (SAW) kuti akhale Mthenga wachifundo kwa anthu 
ake , ndi kuti Mulungu adzamsunga ngati anthu atamuukira. 




Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



389 



\ • *>» 



^ ijjsii 0jj-») 



Surat At-Taubah IX 






1. Uku ndikudzipatula 
kochokera kwa Mulungu ndi 
Mtumiki wake Ku (mapanganowa) 
amene mudapangana nawo 
(Kenako nkuswa mapangano 
awowo) Am'gulu la Amshirikina. 1 

2. (Auze Amshirikina kuti): 
Yendani padziko Miyezi inayi 
basi. (pambuyo pake Sipadzakhala 
chitetezo pakati pawo Ndi ife). 
Ndipo dziwani kuti inu 
Simungathe kumpambana 
Mulungu. Ndipo Mulungu 
Ngosambula osakhulupirira. 

3. Ndipo uku ndi kulengeza 
kochokera Kwa Mulungu ndi 
Mtumiki Wake kwa Anthu pa tsiku 
la Haji Yaikulu kuti Ndithu, 
Mulungu ndi Mtumiki Wake 
Adzichotsa m'mapangano a 
Amshirikina (Omwe ali 
achinyengo). Choncho, ngati 
Mulapa ndibwino kwa inu; ndipo 
ngati Mutembenuka ndi kunyoza, 









tsu 'w<\*9" ii ' "L't^y 









1 Ndime 1-2. Omasulila Qur'an adati Arabu adali kuswa mapangano amene 
adamanga pamodzi ndi Mtumiki wa Mulungu. Potero, Mulungu adalamula 
Mtumiki wake kuti awaponyere mapangano awo. Choncho, Mtumiki adatuma 
Abubakari kukhala mtsogoleri wa anthu kumapemphero a Haji. Ndipo 
adamtsatanso Ali kumeneko ndi nkhani yokhayokhayo kuti akawawerengere 
anthu kuti Mulungu ndi Mtumiki wake atulukamo m'mapangano okhalirana 
mwamtendere ndi Amshirikina sadzaloledwa kuyandikira Nyumba Yopatulika 
chaka chotsatiracho, ndikutinso sadzaloledwa kuzungulira Nyumba 
yopatulikayo uku ali maliseche. 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



390 



\ • frj*-i 



^ hy6\ $jj-*> 



dziwani Kuti inu 
simungamulepheretse Mulungu. 
Ndipo auze za chilango chowawa 
Amene sadakhulupirire. 

4. Kupatula ena amene 
mudapangana nawo Mapangano 
mwa Amshirikina, (omwe 
Adasunga mapangano awo), 
kenako sadapungule Chilichonse 
ndipo sadathandize Aliyense pa 
inu, akwaniritseni Mapangano awo 
mpaka m'nyengo yawo. Ndithu, 
Mulungu akukonda amene 
Akumuopa (ndi kusunga 
mapangano). 

5. Ndipo miyezi yopatulika 
ikatha (Yomwe njoletsedwa 
kuchitamo Nkhondo), apheni 
Amshirikina Paliponse pamene 
mwawapeza (Menyanani nawo), 
ndipo agwireni (Monga momwe 
iwo akukuchitirani). Ndipo 
azungulireni ndi kuwakhalira Pa 
njira zonse. Koma akalapa 
Nayamba kupemphera Swala, 
Ndikupereka chopereka (zakat), 
ilekeni Njira yawoyo (asiyeni). 
Ndithu, Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachisoni. 

6. Ndipo ngati mmodzi wa 
Amshirikina Atakupempha 
chitetezo (kuti amvere Mawu a 
Mulungu), mtetezeni kuti amve 
Mawu a Mulungu. Kenako (ngati 















Surat 9. At-Taubah Juzu 10 I 391 I \ . *> 



^ hjs}\ djf*t 



Sadakhutitsidwe nawo), mpititseni 
Kumalo kwake mwamtendere 
(ngati Safuna kulowa 
m'Chisilamu). Izi Nchifukwa 
chakuti iwo ndi anthu Osadziwa. 

7. Chingakhalepo bwanji 
chipangano Pakati pa Amshirikina 
(oswa Mapangano nthawi ndi 
nthawi) ndi Mulungu ndi Mthenga 
Wake, kupatula Okhawo amene 
mudapangana nawo Mapangano pa 
Msikiti Wopatulika? (Amene 
adakwaniritsa mapangano awo). 
Ngati iwo akupitiriza kulungama 
(Posunga mapanganowo) kwa inu, 
Nanunso pitirizani kulungama kwa 
Iwo. Ndithu, Mulungu akukonda 
amene akumuopa. 

8. (Kodi inu ndiye osunga 
malonjezo?) Bwanji? Pomwe iwo 
akakhala ndi Mphamvu pa inu 
sakusungirani chibale Kapena 
pangano. Amakusangalatsani Ndi 
pakamwa pawo pomwe mitima 
Yawo ikukana (kukukondani). 
Ndipo Ambiri aiwo ngoukira 
malamulo a Mulungu. l 

9. Asinthanitsa aya za Mulungu 
(ndi zinthu Zadziko lapansi) ndi 
mtengo wochepa, Ndipo 
atsekereza (anthu) kunjira Yake. 









" A"\X JO. »WAS 







(^^^J^^ZfOsofc 



X'^tswt 






Mulungu akuti kodi mungapangane nawo mapangano anthu oti akapeza 
mwawi wokugonjetsani inu sasunga chibale chomwe chidali pakati panu 
ngakhale pangano? Iwo amakunenerani mawu otsekemera ngati uchi pomwe 
mitima yawo ndi yodzadzidwa ndi mkwiyo ndi inu. 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



392 



^ • *>i 



^ fajd\ &jy~* 



Ndithu, nzoipa kwabasi zomwe 
Iwo akhala akuchita. 

10. Sasunga chibale pa Msilamu 
ngakhale Pangano. A wo ndiwo 
Opyola malire. 

11. Koma ngati alapa nayamba 
kupemphera Swala ndikupereka 
chopereka (zakaat), Ndiye kuti ndi 
abale anu pa chipembedzo. Ndipo 
tikuzifotokoza ayazi (mwabwino) 
Kwa anthu odziwa. 

12. Ndipo ngati aswa 
malumbiro awo Pambuyo 
pomanga chipangano Chawo, ndi 
kuyamba kutukwana Chipembedzo 
chanu, menyanani nawo Atsogoleri 
akusakhulupirira. Ndithu, iwo 
alibe Mapangano, (sasunga 
mapangano. Menyanani nawo) kuti 
iwo aleke (Machitidwe awo oipa). 

13. Kodi nchotani kuti 
musamenyane Nawo anthu omwe 
aswa malonjezo Awo, natsimikiza 
kumtulutsa (Kumpirikitsa mu 
Mzinda wa Makka, Kapena 
kumupha) Mtumiki? Iwo ndi 
Amene adayamba kukuputani 
Pachiyambi nanga mukuwaopa 
chotani? Mulungu ndiye wofunika 
kumuopa, ngati Inu mulidi 
okhulupirira. 

14. Menyanani nao; Mulungu 
awalanga Kupyolera m'manja anu, 
ndipo Awasambula ndi 



©/ 



• 9\*9' \9\ 



'U. 






S&&T 












Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



393 



> • i£\ 



^ i>jjl Ojj^d 



kukupulumutsani Kwa iwo ndi 
kuchiritsa kuwawidwa (komwe 
Kudali) m'mitima mwa Asilamu 
(Chifukwa cha masautso omwe 
Adawapeza kwa iwo). 

15. Ndi kuchotsa mkwiyo wa 
m'mitima Mwawo (Asilamu). Ndi 
kuti Mulungu Alandire kulapa 
kwa amene wamfuna. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa, Ngwanzeru 
zakuya. 

16. Kodi mukuganiza kuti 
mungosiidwa Chabe Mulungu 
asanawaonetsere Poyera amene 
amenyera chipembedzo Mwa inu 
ndi amene sachita ubwenzi (Ndi 
wina wake) kupatula Mulungu Ndi 
Mtumiki wake ndi Asilamu? 
Ndipo Mulungu Ngodziwa zonse 
zimene Muchita. 

17. Nkosayenera kwa 
Amshirikina Kukhala (ndi udindo) 
woyang'anira Misikiti ya Mulungu 
pomwe iwo Akudzichitira okha 
umboni kuti Ngosakhulupirira. 
Awo (ndi omwe) Zochita zawo 
zabwino zapita pachabe. Ndipo 
iwo ku moto adzakhala Muyaya. 

18. Ndithu, oyang'anira Misikiti 
Ya Mulungu ndi kuiyendera ndi 
Amene akhulupilira Mulungu ndi 
Tsiku lomaliza, ndi kumapemphera 
Swala ndi kupereka chopereka 
(Zakaat) ndipo saopa aliyense 


















Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



394 



1 • *>< 



^ <bjjl Sjj-** 



koma Mulungu yekha. Choncho, 
iwowo Ndi amene 
akuyembekezeka Kukhala mwa 
oongoka. 

19. Kodi kumwetsa madzi 
(anthu) Ochita Haji ndi kusunga 
Msikiti Wopatulika mukukuyesa 
kuti nkofanana Ndi yemwe 
wakhulupirira Mulungu ndi tsiku 
lomaliza, ndi Kumenyera nkhondo 
pa njira Ya Mulungu? Sangakhale 
ofanana Kwa Mulungu.Ndipo 
Mulungu saongola anthu ochita 
zolakwa. 

20. Amene akhulupirira, ndi 
kusamuka, Ndi kumenya nkhondo 
pa njira ya Mulungu ndi chuma 
chawo ndi Matupi awo, ali ndi 
ulemerero Waukulu kwa Mulungu. 
Iwowo ndiwo opambana. 

21. Mbuye wawo akuwauza 
nkhani yabwino Ya chifundo 
chochokera kwa lye, ndi Chiyanjo 
(Chake) ndi minda Yomwe mkati 
mwake adzapezamo Mtendere 
wamuyaya: 

22. Adzakhala m'menemo 
muyaya. Ndithu Mulungu ali nawo 
Malipiro akulu. 

23. E inu amene 
mwakhulupirira! Musawachite 
makolo Anu ndi abale anu kukhala 
Atetezi anu ngati (iwo) akukonda 
Kusakhulupirira Mulungu m'malo 












Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



395 I > • *j*-i 



^ hj£\ Qjj~* 



Mokhulupirira (kukhala Asilamu). 
Ndipo mwa inu amene ati 
awasankhe Kukhala atetezi, otero 
ndiwo adzichitira okha Zoipa. 

24. Nena: "Ngati makolo ami, 
ana Ami abale anu,akazi anu, ndi 
Anansi anu ndi chuma chimene 
Mwachipata,ndi malonda anu 
amene Mukuopa kuti 
angaonongeke, ndi Nyumba zanu 
zimene mukuzikonda, (Ngati 
zinthuzi zili) zokondeka Kwambiri 
kwa inu kuposa Mulungu ndi 
Mtumiki Wake ndi kuchita Jihadi 
pa Njira Yake,choncho dikirani 
kufikira Mulungu adzabwera ndi 
lamulo lake (Lokukhaulitsani). 
Ndipo Mulungu Satsogolera anthu 
otuluka m'chilamulo (Chake). 

25. Ndithu,Mulungu wakhala 
akukupulumutsani (Kwa adani 
anu) m'malo ambiri omenyanira 
Nkhondo, ndi patsiku la Hunaini, 
pamene Kudakunyengani 
kuchuluka kwanu. Koma 
sikudakuthandizeni chilichonse. 
Ndipo dziko lidakupanani 
ngakhale Kuti lidali lotambasuka 
ndipo kenako Mudatembenukira 
kumbuyo (kuthawa). 1 



6^2&jftifcS!& 












Apa Mulungu akuwakumbutsa Asilamu kuti wakhala akuwapulumutsa 
m'nkhondo zosiyanasiyana, makamaka pankhondo ya Hunaini pamene 
Asilamu adali kudzitama kuti sangagonjetsedwe chifukwa cha kuchuluka 
kwawo. Koma kuchulukako sikudawathandize chilichonse. Nthawi zonse 
chofunika kwa Msilamu nkudalira Mulungu. Asadalire mphamvu zake, chuma 
kapena zina zotero. 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



396 



1 * >>i 



^ AjjsJl ^jj- - 



26. Kenaka Mulungu adatsitsa 
mpumuloWake Kwa Mtumiki 
Wake ndi kwa okhulupirira. Ndipo 
adatsitsa asilikali ankhondo a 
(Angelo) omwe simudawaone. 
Ndipo Adawakhaulitsa 
osakhulupirira. Imeneyo Ndiyo 
mphoto ya osakhulupirira. 

27. Ndipo pambuyo pa 
izi,Mulungu Alandira kulapa 
kwawo amene Wamfuna mwa 
osakhulupirira (Powalowetsa 
m' Chi silamu). Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka Ngwachisoni. 

28. "E inu amene 
mwakhulupirira! Ndithu, 
Amushirikina ndi nyansi, 
Choncho, asayandikire Msikiti 
Wopatulika chikatha chaka 
chaochi (cha 9 A.H), Ngati 
mukuopa umphawi, posachedwa 
Mulungu Akulemeretsani ndi 
zabwino Zake akafuna. Ndithu, 
Mulungu Ngodziwa zonse kwabasi 
Ngwanzeru zakuya. 

29. Menyanani ndi omwe 
sakhulupirira mwa Mulungu ndi 
tsiku lomaliza, omwenso Sakusiya 
zoletsedwa zomwe Mulungu Ndi 
Mtumiki Wake waletsa; omwenso 
Satsatira chipembedzo choona 
mwa amene Adapatsidwa mabuku. 
(Menyanani nawo) Kufikira 
apereke msonkho ndi manja awo 
Uku ali odzichepetsa. 



^^^s^mn 



* 



^*^&#i<K 


















Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



397 



> • *>t 



^ AjjsJt SjJ-*> 



30. Ndipo Ayuda akunena kuti 
Uzairi Ndi mwana wa Mulungu, 
naonso Akhrisitu akunena kuti 
Mesiya (Yesu) ndi Mwana wa 
Mulungu. Awa ndi mawu amene 
akunena Ndi pakamwa pawo 
(popanda umboni Wochokera kwa 
Mulungu); Akutsanzira zonena Za 
omwe sadakhulupirire kale. 
Mulungu Awaononge; Kodi iwo 
akusokera chotani Kusiya 
choonadi? 

31. Ayesa ophunzira a za 
chipembedzo Chawo ndi ansembe 
awo kukhala Milungu kusiya Allah 
(powatsata pazimene 
Akuwalamula popanda umboni wa 
Mulungu). (Amsandutsanso) 
Mesiya (Yesu) mwana wa Maria 
(Kukhala Mulungu); chikhalirecho 
Sadalamulidwe china koma 
kupembedza Mulungu Mmodzi. 
Palibe wopembedzedwa 
Mwachoonadi koma lye, 
wapatukana ndi Zimene 
akumphatikiza nazozo. 

32. Akufuna kuzimitsa kuunika 
kwa Mulungu (chisilamu) ndi 
pakamwa Pawo; ndipo Mulungu 
sadzalola Koma kukwaniritsa 
kuunika Kwake Ngakhale kuti 
osakhulupirira zikuwanyansa. 

33. lye ndi Yemwe adatuma 
Mtumiki Wake ndi ulangizi 
ndiponso Chipembedzo choona 



•• 












Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



398 



1 • *J*-I 



^ <UjsJl 3j^-*» 



kuti achiwonetsere Pa zipembedzo 
zonse,ngakhale atanyansidwa nazo 
Amshirikina. 

34. E inu amene 
mwakhulupirira! Ndithu, ambiri 
ophunzira a za Chipembedzo cha 
Chiyuda ndi a za Chikhristu, 
akudya chuma cha anthu 
Mwachinyengo ndikuletsa anthu 
ku Njira ya Mulungu. Ndipo 
amene Akusonkhanitsa golide ndi 
siliva Popanda kuzipereka pa njira 
ya Mulungu, Auze nkhani ya 
chilango chowawa. 

35. Pa tsiku lomwe (chuma 
chawo) Chidzatenthedwa ku moto 
wa Jahannama, ndipo ndi 
chumacho Zidzatenthedwa nkhope 
zawo,nthiti Zawo ndi misana yawo 
(ali kuwuzidwa Kuti): "Izi ndi zija 
zomwe mudadzisungira Nokha. 
Choncho lawani (chilango) Cha 
zomwe mudali kuzisunga. 1 

36. Ndithu,chiwerengero cha 
miyezi Kwa Mulungu (pachaka), 
ndi Miyezi khumi ndi iwiri 
m'chilamulo Cha Mulungu 
kuyambira tsiku lomwe Adalenga 
thambo ndi nthaka. M'menemo 
muli miyezi inayi Yopatulika. Ichi 
ndicho chipembedzo Cha Mulungu 









^loclfe^£!l SvX^(|>j, 



yui^S&'&U-* 6 - 






1 Mu aya iyi, Mulungu akuchenjeza amene akusonkhanitsa chumacho 
nkumangochiunjika m'nkhokwe popanda kutulutsamo chopereka (zakaat). 
Akawalanga nacho pa tsiku la chimaliziro ndi chilango chamoto. Tero, 
tulutsamoni zakat m'chuma chanu. Musanyozere lamulo la Mulungu. 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



399 



1 • *>» 



^ 4jjSj\ djj~*> 









cholunjika. Choncho, 
Musadzichitire nokha zoipa 
m'menemo, Ndipo menyanani ndi 
Amshrikina nonse Pamodzi monga 
momwe akumenyana Nanu onse 
pamodzi. Ndipo dziwani Kuti 
Mulungu ali pamodzi ndi oopa. l 

37. Ndithu, kutalikitsa ndi 
kuchedwetsa (Mwezi wopatulika 
kuti usafike Mwamsanga), 
kumaonjezera kusakhulupirira 
(Mwa Mulungu) Zoterozo 
akusokera nazo amene 
sadakhulupirire. Chaka china 
amauyesa wosapatulika Pomwe 
chaka china amauyesa Wopatulika 
ndi cholinga chokwaniritsa 
Chiwerengero cholingana ndi 
miyezi Yomwe Mulungu 
adaipatula kukhala yopatulika. 
Choncho, chimene Mulungu 
adaletsa, Amachiyesa chololedwa. 
Zakometsedwa kwa Iwo zochita 
zawo zoipa. Ndipo Mulungu 
Sawatsogolera anthu 
osakhulupirira. 2 



1 Chiwerengero chamiyezi m'chaka, ndi khumi ndi iwiri monga mwalamulo la 
Mulungu. M'miyeziyi muli miyezi inayi yopatulika yomwe ndi Rajabu, Zuli 
kada, Zuli Haji ndi Muharamu. M'miyeziyi nkosaloledwa kuchita nkhondo 
pokhapokha mutaputidwa ndi adani. 

Kuichedwetsa miyezi yopatulika, kapena ina mwaiyo ndi kuichotsa 
mumndondomeko wake umene Mulungu adaiika monga momwe ankachitira 
anthu am'nyengo yaumbuli, kumawaonjezera kusakhulupirira anthu 
osakhulupirira mwa Mulungu. Arabu m'nyengo yaumbuli amauyesa mwezi 
wopatulika kukhala wosapatulika akafuna kuti achite nkhondo m'mweziwo. 
Ndipo mwezi wosapatulika amauyesa wopatulika ncholinga choti akwaniritse 
chiwerengero cha miyezi yopatulika yomwe Mulungu adaipatula. Zonsezi 
zimachitika pofuna kukwaniritsa zilakolako zawo zoipa. 



Siirat 9. At-Taubah Juzu 10 



400 



\ * *>» 



^ <OjsJl Qjj* 1 * 



38. E inu amene 
mwakhulupirira! Mwatani; 
mukauzidwa (kuti): "Pitani 
mukachite Jihadi pa Njira ya 
Mulungu, Mukudziremetsa 
panthaka (Polemedwa ndi 
kutulukako)? Kodi 
Mwasangalatsidwa ndi moyo 
wapadziko lapansi Kuposa moyo 
watsiku lomaliza? Koma 
Zosangalatsa za m'moyo wadziko 
Lapansi (poyerekeza ndi moyo wa) 
Tsiku lomaliza, ndi zochepa 
Kwambiri. 

39. Ngati simupita, akulangani 
ndi Chilango chowawa, ndipo 
abweretsa Anthu ena m'malo mwa 
inu; ndipo Simungamuvutitse ndi 
chilichonse (Ngati musiya kupita 
kukamenyanira Panjira yake). 
Ndipo Mulungu Ngokhoza 
chilichonse. 

40. Ngati simumthandiza 
(Mtumuki Muhammad 
{SAW}palibe kanthu), ndithu 
Mulungu adamthandiza pamene 
adamtulutsa Aja amene 
sadakhulupirire. Pamene Adali 
awiriwiri kuphanga Pamene 
ankanenakwa mnzake: 
"Usadandaule. Ndithu, Mulungu 
ali Nafe pamodzi." Ndipo 
Mulungu adatsitsa mpumulo Wake 
pa iye, ndipo Adaamthangata ndi 
asilikali ankhondo Omwe 






®G* 






. jA afcujl %fla> \j3i ijj^^yi 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



401 



1 * *>» 



% ijjsJl 5jj-" 



simudawaone. Ndipo mawu a 
Amene sadakhulupirire adawachita 
Kukhala apansi ndipo mawu a 
Mulungu ndiwo apamwamba. 
Ndipo Mulungu Ngopambana, 
Ngwanzeru zakuya. 

41. Pitani (mukamenyane) muli 
opepuka Ndi olemedwa (anyamata 
ndi Nkhalamba); menyerani njira 
Ya Mulungu nchuma chanu ndi 
Inu nomwe. Zimenezi nzabwino 
Kwa inu ngati muli anthu odziwa. 

42. Ukadakhala ulendo 
wokafuna Zam'dziko zopepuka, 
kuzipeza, ndi Ulendo wofupika, 
ndithu akadakutsata 
(Amunafikuna). Koma ulendo 
Wamavutowu wakhala wautali 
kwa iwo. Ndipo iwo alumbirira 
Mulungu (Ponena kuti): 
"Kukadakhala Kotheka kwa ife, 
tikadapita nanu". (Pamawu awa), 
akudziononga okha. Ndipo 
Mulungu akudziwa kuti iwo 
Ngabodza. 

43. Mulungu wakukhululukira. 
Bwanji Wawaloleza kutsalira? 
(Ukadayembekeza) Kufikira 
adziwike kwa iwe Amene akunena 
zoona, ndikuti Uwadziwe abodza. 

44. Sangakupemphe chilolezo 
(Chotsala kunkhondo) amene 
Akhulupirira mwa Mulungu ndi 
tsiku Lomaliza kuti asapite 












Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



402 



\ * *>i 



^ h$A\ 3jj-*» 



kukamenyera (chipembedzo Cha 
Mulungu) ndi chuma chawo ndi 
Matupi a wo. Ndipo Mulungu 
Akuwadziwa amene akumuopa. 

45. Amakupempha chilolezo aja 
amene Sakhulupirira Mulungu ndi 
tsiku La Chimaliziro, ndipo mitima 
Yawo yakaikira, ndipo iwo, 
Chifukwa cha kukaika kwawo, 
Akungotekeseka. 

46. Akadafunadi kuti atuluke 
(Kupita ku nkhondo) 
akadakonzekera Zokonzekera za 
kunkhondo; koma Mulungu 
sadafune kuti iwo apiteko; 
Choncho adawatsekereza, ndipo 
Kudanenedwa: "Khalani pamodzi 
ndi Otsalira". 

47. Ngati akadatuluka nanu 
pamodzi, Sakadakuonjezerani 
chilichonse Koma chisokonezo 
ndikuyenda Mwaukazitape pakati 
panu Ndicholinga chokufunirani 
chisokonezo, Ndipo mwa inu alipo 
akuwamverera Ndipo Mulungu 
Ngodziwa za oipa. 

48.Ndithudi, akhala 
akukufunirani chisokonezo 
Kuyambira kale, 
akusanthulirasanthulira Zinthu 
(n'cholinga choti athane nawe) 
Kufikira choonadi chadza 
ndikuonekera Poyera lamulo la 
Mulungu (lowakhaulitsa Ayuda) 
iwo asakufuna. 



ei^fc»fc&**4Wi 












1 ' 



*&jj^&\$&<& 






Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



403 



> • *>i 



^ 4j asjI 6j J""* 






o oil u3 lyy£| 2u£*9* <^U*f? 






49. Ndipo mwa iwo pali yemwe 
akuti: "Ndiloreni ine (kuti nditsale 
kunkhondo) Ndipo musandiponye 
m'mayeso (kuopa Kuti 
ndingalakwe ndikaona akazi 
Akumeneko)" Ndithudi, iwo agwa 
kale M'mayesero. Ndipo, ndithu, 
Jahannama Ikawazinga mbali 
zonse osakhulupirira. 

50. Chikakupeza chabwino, 
(iwe Mtumiki Muhammad (SAW) 
ndi okutsatira) zimawanyansa 
Ndipo vuto likakupeza amanena, 
"Tidalingalira zinthu zathu kale. 
(Nchifukwa chake mavuto 
atizemba). Ndipo amatembenuka 
nkupita uku Akukondwa. l 

Sl.Nena: "Palibe chomwe 
chitipeze koma Chimene Mulungu 
watilembera. lye Ndi Mbuye 
wathu". Choncho, Asilamu 
Ayadzamire kwa Mulungu yekha. 

52. Nena: "Kodi chilipo 
chimene Mukuyembekezera mwa 
ife posakhala Chimodzi mwa 
zinthu ziwiri zabwino, 
(Kupambana pankhondo 
ndikupeza Zotolatola zake, kapena 
kufa Ndikukalowa ku Munda wa 
Mtendere)? Ndipo nafe 
tikukuyembekezerani kuti 
Mulungu akupatsani chilango 



1 Achinyengo sadali kufunira zabwino Asilamu ngakhale kuti adali 
kudzipachika m'gulu la Asilamu mwachinyengo. Ankati vuto likawagwera 
Asilamu amasangalala. Koma chikawadzera chabwino amadandaula. 






' 9 9 <>'6 9 k ' *\f- 









Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



404 



\ • *>» 



^ 4jjiJl djj-*» 



Chochokera kwa lye, kapena 
kupyolera M'manja mwathu. 
Choncho Bayembekezerani; 
nafenso Tikuyembekezera nanu 
limodzi". 

53. Nena (kwa Amunafikina): 
"Perekani (Chuma chanu) 
mwachifuniro kapena Mosafuna 
sichizalandiridwa kwa inu. 
Ndithu, inu ndinu anthu Otuluka 
m'chilamulo cha Mulungu". 

54. Palibe chomwe chidaletsa 
kulandiridwa Kwa zopereka zawo 
koma chifukwa Chakuti iwo 
sadakhulupirire Mulungu Ndi 
Mtumiki Wake; ndiponso sapita 
Kopemphera koma mwaulesi; 
ndipo Sapereka chopereka Koma 
monyinyirika. 

55. Ndipo chisakudolole chuma 
chawo Kapena ana awo. Ndithu, 
Mulungu Akufuna kuwalanga nazo 
pamoyo Wapadziko lapansi, ndi 
kuti mitima Yawo ichoke ali 
osakhulupirira. 

56. Akulumbira (m'dzina la) 
Mulungu Kuti iwo ali pamodzi ndi 
inu; Pomwe iwo sali pamodzi nanu 
koma iwo Ndi anthu amantha. 

57. Ngati akadapeza linga 
lothawiramo Pena mapanga 
kapena pamalo pena Polowa 
(ndithu) akadathawira kumeneko 
Mwa liwiro. 






9 9t,l<<9 99 *\'Z.& >< 9*"S\" 









Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



405 



\ • *>i 



\ hj£\ djj-*> 



58. Ndipo alipo ena mwa iwo 
(Amunafikina) amene akukunena 
(Mkugawa kwako) sadaka: 
akapatsidwa Kanthu m'menemo 
amakondwera koma Akapanda 
kupatsidwa akukwiya nawe. 

59. Ngati iwo akadakondwera 
ndi chimene Mulungu ndi Mtumiki 
Wake wawapatsa, Nanena: 
"Mulungu watikwanira. 
Posachedwapa Mulungu ndi 
Mtumiki Wake atipatsa zabwino 
Zake. Ndithu, ife tikufunitsitsa 
kwa Mulungu." (Ndiye kuti 
Mulungu Akadawapatsa zambiri). 

60. Ndithu,zakati ndi ya 
mafukara, Masikini, ogwira ntchito 
yosonkhetsa Zakatiyo, owalimbitsa 
mitima yawo (Pa chisilamu amene 
alowa kumene), Kuombolera 
akapolo kuti akhale mfulu, 
Kuthandizira amene ali 
m'ngongole; Kuipereka pa njira ya 
Mulungu; Ndi kuwapatsa 
apaulendo (omwe alibe 
Choyendera). Hi ndi lamulo 
lochokera kwa Mulungu, ndipo 
Mulungu Ngodziwa Kwabasi, 
Ngwanzeru zakuya. 






©<a 



" 9 S?Z 9 ' 9>\<&9 



% 









©: 



M'ndime iyi Mulungu akutifotokozera magulu a anthu amene ngoyenera 
kuwagawira chuma cha zakati. Iwo ndi awa:- 

1 . Osauka amene alibe zokwanira pa zofunikira pa moyo wawo. 

2. Osauka amene sangagwire ntchito nkudzipezera okha chakudya (Masikini). 

3. Amene akusonkhetsa chuma cha zakaticho omwe ntchito yawo 
ndiyokhayo. 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



406 



1* *>» 



^ ijjjl Ojj-j 



61. Ndipo alipo ena mwaiwo 
amene Akuzunza Mneneri ponena 
kuti: "Uyu ndi khutu (lomvetsera 
nkhani Iliyonse popanda 
kuiganizira)" Nena: "Ndi khutu 
labwino kwa inu". (Mwini 
khutulo) amakhulupirira Mulungu: 
Amakhulupirira (Zonena) za 
Asilamu, ndipo (iye) Ndi mtendere 
kwa amene akhulupirira Mwa inu. 
Ndipo amene akuvutitsa Mtumiki 
wa Mulungu adzakhala ndi 
Chilango chopweteka. 

62. Akulumbira kwa inu 
potchula Dzina la Mulungu kuti 
akukondweretseni (Chikhalirecho 
akunyoza Mulungu ndi Mtumiki 
Wake), pomwe Mulungu ndi 
Mtumiki Wake ndiye Wofunika 
kuti amkondweretse ngati Iwo 
ngokhulupiriradi (mwachoonadi). 

63. Kodi sadziwa kuti amene 
akulimbana Ndi Mulungu ndi 
Mtumiki Wake, adzapeza Moto wa 
Jahannama Ndi kukhalamo 
muyaya? Kumeneko Ndi kuyaluka 
kwakukulu. 

64. Amunafikina akuopa 
kuwatsikira Sura yomwe 















4. Amene angolowa kumene m'Chisilamu omwe akuyembekezedwa kuti 
akapatsidwa adzalimbikitsidwa mitima yawo pachipembedzochi. 

5. Amene afuna kudziombola ku ukapolo. 

6. Amene akulephera kulipira ngongole ya choonadi. 

7. Amene akuchita Jihadi panjira ya Mulungu. 

8. Wapaulendo amene alibe choyendera (ndalama zoyendera). 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



407 



S * *>» 



^ 4jj^it *j>**' 



ingawafotokozere (Zachinyengo 
chawo) chomwe chili M'mitima 
mwawo. Nena: "Chitani 
Zachipongwe. Ndithu, Mulungu 
atulutsira Poyera zomwe 
mukuziopazo (kuti Asilamu 
Asazidziwe). 

65. Ndipo utawafunsa 
(chifukwa ninji Chipembedzo 
akuchichitira Chipongwe)?Anena: 
"Ife timangosereula Ndi kusewera 
basi (palibe china)." Nena: 
"Mumachitira Mulungu ndi aya 
Zake ndi Mtumiki Wake 
zachipongwe?" 

66. Musapereke madandaulo 
(abodza) Ndithu mwaonetsera 
ukafiri wanu Poyera, pambuyo 
pakukhulupirira Kwanu 
(kwabodza). Ngati gulu lina mwa 
inu Tilikhululukira (litalapa), gulu 
lina tililanga Chifukwa cha 
kupitiriza kulakwa kwawo. 

67. Amunafikina aamuna ndi 
Amunafikina Aakazi onse 
khalidwe lawo ndi Limodzi. 
Amalamulira zoipa ndikuletsa 
Zabwino, ndipo amafumbata 
manja awo (Sathandiza 
pazabwino). Amuiwala Mulungu 
(Ponyozera malamulo Ake). 
Iyenso wawaiwala (Powanyozera). 
Ndithu, Amunafikina ngotuluka 
M'chilamulo cha Mulungu. 



-^^V- 






Tip" 









£y£»*s£*> <LjL&i$J <&*£$ 

'" 9 *" X 9 A\ ' >9> 9 x's **' 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



408 



\ • *>i 



^ 4jjsJI 5jJ-*» 



68. Mulungu walonjeza 
Amunafikina aamuna Ndi 
Amunafikina aakazi ndi Akafiri, 
Moto wa Jahannama, akakhala 
m'menemo Muyaya. Umenewo 
ukukwanira Kwa iwo (kuwalanga). 
Ndipo Mulungu Wawatemberera, 
ndipo iwo adzapeza Chilango cha 
nthawi zonse. 

69. (Inu osakhulupirira) ndinu 
ofanana Ndi amene adalipo 
patsogolo panu. (Tikuonongani 
monga tidawaonongera Iwo; 
koma) iwo adali ndi nyonga 
Zambiri kuposa inu; adalinso ndi 
chuma Chambiri ndi ana ambiri 
kuposa inu. Choncho, 
adasangalalira gawo lawo Inunso 
mukusangalalira gawo lanu Monga 
momwe adasangalalira gawo lawo 
omwe Adalipo patsogolo panu, 
ndipo mwamira M'zoipa monga 
momwe adamirira iwo. A wo ndi 
amene zochita zawo zidapita 
Pachabe padziko lapansi ndi 
patsiku Lomaliza. Awo ndi omwe 
ali otaika. 

70. Kodi siidawadzere nkhani 
ya amene Adalipo patsogolo pawo, 
anthu a Nuhi, Adi ndi Samudu; 
anthu a Ibrahim Ndi anthu a ku 
Madiyana ndi (anthu) a M'Midzi 
imene idatembenuzidwa 
Kumwamba kukhala pansi, pansi 
kukhala Kumwamba? Atumiki 















Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



409 1 • *>■» 



H AJJ^I <*JJ~" 



awo adawadzera ndi Zisonyezo 
zoonekera (koma adakana 
Kuwatsata.Choncho, Mulungu 
adawaononga). Mulungu 
sadawachitire choipa, koma 
Ankadzichitira okha zoipa. 

71. Okhulupirira aamua ndi 
okhulupirira Aakazi, ndiabwenzi 
omvana pakati Pawo. Amalamula 
zabwino ndikuletsa zoipa ndipo 
Amapemphera swalandi 
Kupereka chopereka (zakaat), ndi 
Kumvera Mulungu ndi Mtumiki 
wake. Awo ndi omwe Mulungu 
adzawachitira Chifundo. Ndithu, 
Mulungu Ngwamphamvu Zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 

72. Mulungu waalonjeza 
okhulupirira aamuna Ndi 
okhulupirira aakazi Minda yomwe 
pansi Ndi patsogolo pake mitsinje 
Ikuyenda adzakhala m'menemo 
nthawi zonse. Ndi mokhala 
mwabwino m' Minda ya nthawi 
Zonse (yosatha) .Ndipo chiyanjo 
Chochokera kwa Mulungu ndi 
chachikulu (Omwe ndi mtendere 
waukulu kwambiri Kuposa zonse). 
Kumeneko ndiko kupambana zedi. 

73. E iwe Mneneri! Limbana 
ndi Osakhulupirira ndi 
Amunafikina ndipo uwaumire 
mtima. Mbuto yawo ndi ku 
Jahannama. Taonani kuipa kwa 
Malo obwelera. 



' 999 *?* 'K»'*ll < '9*9'* 









99 **. S9y * 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



410 \> ' *>' 



S 3->jiJt &JJ** 



74. (Amunafikina pambuyo 
pomunenera Mulungu ndi Mtumiki 
Wake mawu Oipa), akulumbira 
potchula dzina La Mulungu (kuti) 
sadanene (Zonyoza), pomwe 
adanenadi mawu Aukafiri, ndipo 
akana chikhulupiriro pambuyo 
posonyeza Chisilamu Chawo 
(chabodza); ndipo adatsimikiza 
(kuchita) zomwe sadathe Kuzifika. 
Komatu sadaone choipa (M'kudza 
kwa Chisilamu), koma kuti 
Mulungu ndi Mtumiki Wake 
adawalemeretsa Ndi zabwino zake. 
Choncho Ngati alapa, zikhala 
zabwino kwa iwo. Ndipo ngati 
anyoza, Mulungu Awalanga ndi 
chilango chowawa Pamoyo 
wapadziko lapansi ndi Patsiku 
lomaliza. Ndipo sadzakhala Ndi 
mtetezi ngakhale aliyense 
Wowapulumutsa padziko. 

75. Pakati pawo alipo amene 
adalonjeza Mulungu kuti, "Ngati 
atipatsa Zabwino zake (chuma) 
tidzapereka sadaka ndi kukhala 
m'gulu la Ochita zabwino." 

76. Koma pamene adawapatsa 
Zabwino zakezo, adazichitira 
Umbombo nanyoza, 
Natembenukira kutali Ndi 
Mulungu. 

77. Choncho, chotsatira chake 
adawaika Chinyengo m'mitima 
mwawo kufikira Tsiku lokumana 















Siirat 9. At-Taubah Juzu 10 



411 



> • *j*-l 



^ 4jjs)| 9jj**t 



naye (Mulungu), Chifukwa cha 
kuphwanya kwawo zomwe 
Adamulonjeza Mulungu. Ndiponso 
Chifukwa cha zabodza zomwe 
ankanena. 

78. Kodi sadziwa kuti Mulungu 
Akudziwa zobisika zawo ndi 
Manong'onong'o awo Ndikuti 
Mulungu Ngodziwa zinthu 
zamseri? 

79. Amene akuwanena Asilamu 
opereka Sadaka yambiri, ndiponso 
(amene Akunyoza) amene sapeza 
(Chopereka), koma chinthu 
Chochepa; ndikumawachitira 
Chipongwe, Mulungu adzawalipira 
Chipongwe chawocho. I wo 
adzapeza Chilango chopweteka. 

80. (EiweMtumiki!) 
Uwapemphere Chikhululuko 
(Amunafikina) Kapena 
usawapemphere, (zonsezo 
Nchimodzimodzi). Ngakhale 
Utawapemphera chikhululuko 
Chochuluka kwabasi mokwanira 
Makumi asanu ndi awiri (70) 
Mulungu sangawakhululukire. 
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo 
Akana Mulungu ndi Mtumiki 
Wake. Ndipo Mulungu satsogolera 
anthu Ophwanya malamulo Ake. 

81. Akondwa amene adasiidwa 
m'mbuyo (Osapita kunkhondo) 
chifukwa Chakukhala kwawo 



©&>$#£ 









Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



412 



\ * *>i 



^ 4jjiil 0jj-*» 



m'mbuyo Polekana ndi Mtumiki 
wa Mulungu, nakuda kumenyana 
pa Njira ya Mulungu ndi chuma 
chawo Ndi moyo wawo, nati (kwa 
anzawo): "Musapite (kunkhondo) 
m'nthawi Yotenthayi." Auze: 
"Moto wa Jahannama ngotentha 
kwambiri Akadakhala 
akuzindikira." 

82, Choncho, aseke pang'ono 
(padziko Lapansi).Ndipo adzalira 
kwambiri (Patsiku lomaliza); (iyo 
ndi) Mphoto ya zomwe adapeza 
(Kuchokera m'zochita zawo 
zoipa). 1 

83, Ngati Mulungu akubweza 
(kunkhondoko) Nkufika kugulu 
lina la mwa iwo ndipo Iwo 
nkukupempha chilolezo 
chakutuluka (Kupita kunkhondo, 
zomwe Zidzapezeke mtsogolo), 
nena: "Inu Simudzatuluka nane 
mpaka muyaya, Ngakhalenso 
kumenyana ndi adani Pamodzi 
nane; inu mudakonda Kukhala 
nthawi yoyamba; choncho Khalani 
(nthawi zonse) pamodzi Ndi 
otsalira (pambuyo)." 

84, Ndipo usamupempherere 
konse Aliyense wa iwo yemwe 






-'*- 9 <"/\<>$i*\Z\*'' *'* 



*&%&*$> 






~»1* < 






%& 



%\®<&2&£&><&>3S 



Anthu achinyengo (Amunafikina) adakana kupita naye limodzi Mtumiki 
(SAW) kunkhondo namasangalalira kukhala kwawoko. Ndipo apa Mulungu 
akuwauza kuti asangalale ndi kuseka pang'ono. Koma adzalira ndi kukukuta 

monn ntl-f^nii wsi+'sIS 



Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



413 



s « t>l 



^ *ujJl 5jj~»> 



wamwalira, Ndipo usaimirire 
pamanda ake (Kumpempherera); 
ndithu, iwo Amukana Mulungu ndi 
Mtumiki Wake, Ndipo amwalira 
uku ali opandukira Chilamulo cha 
Mulungu. 

85. Ndipo chisakudolole chuma 
cha wo Kapena ana awo. Ndithu 
Mulungu akufuna kuwalanga Ndi 
zimenezo padziko Lapansi, ndi 
kuti mizimu Yawo ichoke ali 
Osakhulupirira. 

86. Ndipo Sura 
ikavumbulutsidwa (yonena 
Kuti):"Mkhulupirireni Mulungu 
ndi kumenya Nkhondo (chifukwa 
cha chipembedzo Chake) Pamodzi 
ndi Mtumiki wake, " Opeza bwino 
mwa Iwo akukupempha chilolezo 
(Kuti asapite kunkhondo), ndipo 
akuti: "Tisiye tikhale pamodzi ndi 
okhala (Otsalira m'mbuyo)." 

87. Akondwera pokhala limodzi 
ndi Otsalira m'mbuyo (akazi ndi 
ana). Ndipo mitima yawo 
yadindidwa chidindo 
(Yatsekedwa), choncho iwo 
sazindikira. 

88. Koma Mtumiki ndi amene 
Akhulupirira pamodzi ndi iye 
Amenya nkhondo Ndi chuma 
cha wo ndi matupi awo. Iwo wo 
ndi wo opeza zabwino, Ndiponso 
iwowo Ndiwo opambana. 















Surat 9. At-Taubah Juzu 10 



414 



) * *>i 



^ iij^l Sjj-j 



89. Mulungu wawakonzera 
minda yoyenda Mitsinje pansi ndi 
patsogolo pake; adzakhala 
M'menemo muyaya. Kumeneko 
ndiko Kupambana kwakukulu. 

90. Ndipo adza eni madandaulo 
(oona), mwa anthu Am'chipululu 
(omwe ndi Asilamu) kuti 
Awapatse chilolezo (chosapita 
kunkhondo). Koma adakhala 
(popanda kupempha chilolezo 
Kwa Mtumiki ) amene amunamiza 
Mulungu ndi Mtumiki wake. 
(Amenewa ndi Amunafikina omwe 
Amadzitcha kuti ndi Asilamu 
pomwe sadali Asilamu). Mwa iwo 
amene sadakhulupirire Mulungu 
chiwapeza chilango chopweteka. 

91. Palibe tchimo (kusapita 
kunkhondo) Kwa amene ali ofooka 
(pachilengedwe Chawo) ngakhale 
kwa odwala, ngakhale kwa Omwe 
sapeza chothandiza (paulendo 
ngakhale Chosiira akubanja lawo) 
ngati iwo ali ndi Cholinga 
chabwino pa Mulungu ndi 
Mtumiki Wake. Palibe njira 
(yowadzudzulira) amene Akuchita 
zabwino. Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka kwabasi, 
Ngwachisoni. 

92. Ndiponso (palibe tchimo) 
kwa Amene akukudzera kuti 
uwatenge (Kupita kunkhondo) iwe 
uunena: "Ndilibe choti 












Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



415 



> > *>» 



^ 4jy)\ dj^-*> 



ndikunyamulireni," Nabwera maso 
awo Akutuluka misozi chifukwa 
Chakudandaula posapeza zimene 
Zingawathandize paulendowo. 

93. Ndithu, njira 
(yodzudzulidwa) ili pa amene 
Akukupempha chilolezo (choti 
asapite kunkhondo Ndikusiyanso 
kupereka chuma chawo) Pomwe 
iwo ngolemera. Akonda kukhala 
pamodzi Ndi otsala m'mbuyo. 
Ndipo Mulungu wadinda Chidindo 
(chamantha) m'mitima mwawo, 
tero Sadziwa (chilichonse 

cho wathandidza) . 

94. Akudandaulirani 
madandaulo Mukabwerera kwa 
iwo (ndi kukumana Nawo). Nena: 
"Musapereke madandaulo; 
Sitikukhulupirirani. Mulungu 
watifotokozera kale Nkhani zanu. 
Posachedwa Mulungu ndi Mtumiki 
Wake aona zochita zanu, Kenako 
muzabwezedwa (Pambuyo pa 
imfa) kwa Wodziwa Zamseri ndi 
zoonekera. Choncho, lye 
adzakufotokozerani zimene Mudali 
kuchita." 

95. Mukabwerera kwa iwo, 
adzalumbira M'dzina la Mulungu 
kwa inu kuti Muwasiye 
(musawachite kanthu). Choncho, 
apatukireni. Ndithu, iwo Ndi uve 
ndipo malo awo ndi ku Jahannama. 
Iyi ndi mphoto ya Zomwe adali 












Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



416 



U ftjA-i 



h ^jsi* *jj-*' 



kupeza (kuchokera m'zochita 
Zawo zoipa). 

96. Akulumbira kwa inu kuti 
muwayanje Ngati inu muwayanja, 
(dziwani kuti Mulungu 
sakuwayanja). Ndithu, Mulungu 
sayanja anthu otuluka 
M'chilamulo. 

97. Anthu am'chipululu 
ngoyipitsitsa Pakusakhulupirira ndi 
uchiphamaso ndiponso Ngoyenera 
kusazindikira malire a Zomwe 
Mulungu wavumbulutsa kwa 
mtumiki Wake. Komatu Mulungu 
Ngodziwa Kwambiri, Ngwanzeru 
zakuya. 

98. Ndipo alipo ena mwa anthu 
a m'chipululu Omwe amachichita 
chimene Akupereka pa njira ya 
Mulungu Ngati dipo (laulere 
lopanda phindu,) Ndikumadikira 
kwa inu kuti miriri Ikupezeni. 
Miriri yoipa ili paiwo; (Iwapeza 
okha). Ndipo Mulungu 
Ngwakumva (nkhani iliyonse), 
Wodziwa (Chilichonse). 

99. Ndipo alipo ena mwa anthu 
A m'chipululu omwe 
akukhulupirira Mulungu ndi tsiku 
lomaliza ndipo Zomwe akupereka 
(pa njira ya Mulungu) amazichita 
monga Chodziyandikitsira nacho 
kwa Mulungu, ndi (chowachititsa 
kuti Apeze) mapemphero a 












Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



417 



n *>» 



^ i»jJ* Ojj~rf 



mtumiki. Tamverani! Ndithu, 
zimenezo Ndizinthu 
zowayandikitsa kwa Mulungu. 
Mulungu adzawalowetsa 
Kumtendere Wake. Ndithu, 
Mulungu Ngokhululuka kwambiri, 
Ngwachisoni. 

lOO.Ndipo amene adatsogolera 
poyamba, Am'gulu la Amuhajirina 
ndi Answari, ndi omwe 
adawatsatira Iwo mwaubwino, 
Mulungu adzakondwa Nawo. 
Naonso adzakondwera Naye (pa 
Zomwe adzapatsidwa ndi 
Mulungu.) Ndipo wawakonzera 
minda yomwe mitsinje Ikuyenda 
pansipake; adzakhala M'menemo 
muyaya. Uko ndikupambana 
Kwakukulu. 

101* Ndipo ena mwa anthu 
am'chipululu omwe Akukhala 
m'mphepete mwanu (M'mphepete 
mwa mzinda wa Madina) Alipo 
Amunafikina (achinyengo); 
Ndiponso eni Mzinda wa Madina 
Aphunzira ukatswiri wachinyengo 
(Kotero kuti) sukuwadziwa. Ife 
Tikuwadziwa. Tiwalanga kawiri 
(Padziko lapansi). Ndipo kenako 
Adzabwezedwa kuchilango 
chachikulu (Patsiku lomaliza). 

102. Ndipo alipo ena omwe 
avomereza Uchimo wawo (nalapa 
kwa Mulungu). Asakaniza zochita 
zabwino ndi Zina zoipa. Ndithu, 












Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



418 



U fr>» 



^ hyA\ <*jj~»» 



Mulungu Alandira kulapa kwawo. 
Ndithu Mulungu Ngokhululuka, 
Ngwachisoni. 

103. Tenga sadaka m'chuma 
chawo Kuti uwayeretse nayo 
(kumachimo Ndi umbombo) 
ndikuti uwatukulire nayo 
Ulemerero wawo kwa Mulungu; 
ndipo Apemphere ( zabwino ndi 
chiongoko). Ndithu, mapemphero 
ako kwa iwo Ndi mpumulo. 
Ndipo Mulungu Ngwakumva, 
Wodziwa (chilichonse.) 

104. Kodi sadziwa kuti 
Mulungu Amalandira kulapa kwa 
akapolo Ake, ndi kulandira sadaka, 
Ndikuti Mulungu ndi Mwini 
kulandira Kulapa mochuluka 
ndiponso Wachisoni. 

105. Ndipo auze: "Chitani 
(zinthu Zabwino); Mulungu ndi 
Mtumiki Wake ndi Asilamu aona 
zochita Zanuzo posachedwa. 
Ndipo (kenako) Mudzabwezedwa 
kwa Wodziwa zamseri Ndi 
zoonekera poyera. lye adzakuuzani 
Zonse (zimene) mudali kuchita." 

106. Ndipo aliponso ena amene 
(adagwa M'machimo omwe) 
akudikirira Lamulo la Mulungu, 
(kulapa kwawo 

Sikunavomerezekebe), kapena 
Awalanga kapenanso awavomera 
Kulapa kwawo .Ndipo Mulungu 



9 > 9*\'&4'JZ " 9 \\' 9 i 9 9 K 






* 9\'9& 






Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



419 > > >>> 



H *JjA\ ^JJ - "** 



Ngodziwa (Khalidwe lawo ndi 
zomwe zili M'mitima mwawo), 
Wanzeru zakuya (Pazonse zomwe 
akuchita kwa anthu Ake popereka 
mphoto ndi chilango). 

107. Ndipo (alipo Amunafikina 
ena) amene Adamanga msikiti ndi 
cholinga chodzetsa Masautso ndi 
(kulimbikitsa) kusakhulupirira 
Mulungu ndi kuwagawa Asilamu 
(mu umodzi Wawo) ndi kuupanga 
kukhala msasa wa omwe 
Adamthira nkhondo Mulungu ndi 
Mtumiki Wake Kale. Ndithu, 
alumbira (ndikunena): "Sitidali 
ncholinga china (pomanga 
Msikitiwo) koma ubwino." Koma 
Mulungu akuikira umboni kuti iwo 
Ngabodza. 

108. Usaimirire (ndi 
kupemphera) m'menemo 
Mpang'ono pomwe. Ndithu,msikiti 
Umene udakhazikitsidwa poyamba 
Ncholinga choopa Mulungu ndiwo 
Wofunika kuti uimirire m'menemo 
(Ndi kupemphera). M'menemo 
muli Anthu okonda kudziyeretsa 
(matupi Ndi mitima yawo); ndipo 
Mulungu Amakonda odziyeretsa. 

109.Kodi amene wakhazikitsa 
maziko Achomanga chake 
chifukwa choopa Mulungu ndi 
kufunafuna chiyanjo (Chake), 
sindiye wabwino, kapena Yemwe 
wakhazikitsa maziko Achomanga 












Siirat 9. At-Taubah Juzu 11 



420 



) \ tji-i 



^ hjd\ djj~* 



chake m'mphepete mwa Dzenje 
(lakuya) lomwe dothi lake 
Likugumukira (m'dzenjemo) ndipo 
Nkugwa pamodzi naye mmoto wa 
Jahannama, ( ameneyu ndiye 
wabwino?) Ndithudi, Mulungu 
saongolera anthu Ochita zoipa. 

110. Chomanga chawo chomwe 
adachimanga Sichileka kudzetsa 
chikaiko ndi Kusakhazikika 
m'mitima mwawo Kufikira mitima 
yawo itaduka (Ndi madandaulo 
kapena imfa). Ndipo Mulungu 
Ngodziwa (chilichonse), 
Ngwanzeru zakuya 
(M'zochitachita Zake). 

lll.Ndithu, Mulungu wagula 
kwa Asilamu Moyo wawo ndi 
chumachawo (kuti Apereke moyo 
wawo ndi chuma chawo Pomenya 
nkhondo pa njira ya Mulungu) kuti 
iwo alandire Munda Wamtendere. 
Akumenya nkhondo pa Njira ya 
Mulungu, ndipo akupha Ndi 
kuphedwa. Hi ndi lonjezo Loona 
lokakamizika pa lye lomwe 
Likupezeka m'Buku la Taurati, 
Injili ndi Qur'an. Kodi ndani 
Wokwaniritsa lonjezo lake kuposa 
Mulungu? Choncho kondwerani 
ndi Kugulitsa kwanu komwe 
mwagulitsana Naye. Kumeneko 
ndiko kupambana kwakukulu. 

112. (A wo amene alonjezedwa 
kupeza izi, Ndi) omwe amalapa 









£>>xJ>JI 6i^l <z)j?0 



Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



421 



U ftjA-i 



^ 4jjJ| 5jJ-*> 



(akalakwa); Ochita mapemphero 
(awo m'njira Yoyenera); otamanda 
Mulungu Kwambiri; ochulukitsa 
kusala (Swaumu kapena 
oyendayenda padziko Ncholinga 
chochitira zabwino anthu) 
Owerama, ogwetsa nkhope zawo 
pansi; Olamula zabwino; oletsa 
zoipa ndi Osunga malire a 
Mulungu (malamulo Ake). 
Choncho, auze nkhani yabwino 
Awo amene akhulupirira. 

113. Nkosayenera kwa Mneneri 
ndi amene Akhulupirira 
kuwapemphera chikhululuko 
Amushirikina (opembedza 
Mafano) ngakhale atakhala abale 
Awo, pambuyo poonekera Kwa 
iwo kuti iwowo Ndi anthu 
akumoto. 

114.Ndipo Ibrahim 
sadampemphere bambo Wake 
chikhululuko koma chifukwa Cha 
lonjezo lomwe adamulonjeza. 
Koma pamene zidaonekera kwa 
iye Poyera kuti iye (bambo wake) 
ndi Mdani wa Mulungu, 
Adadzipatula kwa iye. Ndithudi, 
Ibrahim adali wochulukitsa 
kupempha Mulungu 
modzichepetsa, woleza mtima. 

HS.Ndipo Mulungu 
sangasokeretse Anthu (ndi 
kupititsa chilango pa iwo) 
pambuyo Powaongolera ku 















Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



422 



U *>i 



^ AjjsJl &jj** 



chisilamu; koma Pokhapokha 
atawonetsa poyera kwa iwo 
Zimene zingafunike kuzipewa 
(Powavumbulutsira chivumbulutso 
Kudzera kwa mtumiki. Koma 
akapanda Kupewa zofunika 
kuzipewa, ndi pomwe 
Amawerengedwa kuti ndi anthu 
oipa). Ndithu, Mulungu Ngodziwa 
chilichonse. 

1 16. Ndithudi,Mulungu ndi 
Wake Ufumu wakumwamba Ndi 
pansi. Amapereka moyo ndi Imfa. 
Inu mulibe mtetezi ngakhale 
Mthandizi koma Mulungu basi. 

117,Ndithu,Mulungu wafunira 
zabwino MtumikiWake ndi 
Amuhajirina ndi Answari amene 
adamtsatira iye 

(Muhammad{SAW}) m'nthawi 
yamasautso (Pokamenyana ndi 
Aroma pankhondo ya Tabuk), 
nthawi yomwe mitima ya ena A 
iwo idatsala pang'ono kupotoka 
(Kutsata machitidwe achikafiri); 
Kenako Mulungu 
adawatembenukira ndi Chifundo. 
Ndithu, Iye (Mulungu). Kwa iwo 
Ngodekha, Ngwachisoni. 1 



«S8^<^&^ 






Nkhondo ya Tabuk idachitika m'mwezi wa Rajab m'chaka cha chisanu 
nchinayi chakusamuka. Idali pakati pa Asilamu ndi Aroma. Gulu lankhondo la 
Chisilamu lomwe lidapita kunkhondo linkatchedwa "Gulu la Masautso" chifukwa 
kukonzekera kwa nkhondoyi kudachitika m'nyengo yamasautso kwa anthu. 
Ndipo pamene Mtumiki adafika ku Tabuk, adadza Yohane namvana kuti 
pasakhale nkhondo. 

M'malo mwake iye adzapereka "Jiziya" (msonkho), motero Mtumiki adabwerera 
ku Madina. lyi idali nkhondo yake yomaliza. 



Siirat 9. At-Taubah Juzu 11 



423 



n tjA-i 



^ ^j^f ^jj"** 



118.Ndiponso 
(adawatembenukira mwachifundo) 
Aja atatu amene adawadikiritsa 
(Pakusavomera msanga kulapa 
kwawo Kufikira pamene dziko 
Lidawapana ngakhale lidali 
lophanuka Nabanika m'mitima 
mwawo Natsimikiza kuti palibe 
Komuthawira Mulungu (kwina) 
Koma kwa lye (Mulungu polapa). 
Kenako (Mulungu) adawatsogolera 
Kulapa kuti alape. Ndithu, 
Mulungu Ngolandira kulapa, 
Ngwachisoni. 

119.E inu amene 
mwakhulupirira! Opani Mulungu: 
ndipo khalani pamodzi ndi oona 
(Amene akuchitsimikiza Chisilamu 
chawo Ndi zochita zawo, osati 
kungoyankhula Pakamwa pokha). 

120.Nkosayenera kwa anthu 
amumzinda Wa Madina ndi amene 
ali M'mphepete mwawo, mwa 
anthu Am'chipululu, kutsalira 
M'mbuyo mwa Mtumiki wa 
Mulungu (poleka Kutsagana naye 
kunkhondo), Ndiponso 
nkosayenera kwa iwo Kudzikonda 
okha kuposa iye (Mtumiki) . 
Zimenezo Nchifukwa choti iwo 
silingaapeze Ludzu kapena mavuto 
kapena Njala pa njira ya Mulungu, 
ndipo Sangaponde malo okwiitsa 
osakhulupirira, Ndipo sangampatse 
mdani Chompatsa chilichonse 












Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



424 



U *>» 



^ hjd\ Ojj-a 



chopweteka Koma kulembedwa 
kwa iwo pa Zimenezo (kuti 
achita) ntchito Yabwino. 
Ndithu,Mulungu sawononga 
Malipiro a ochita zabwino. 

121.Ndipo sangapereke 
chopereka Chaching'ono kapena 
chachikulu, ndipo Sangadutse 
mtunda wachigwa; koma 
Kulembedwa kwa iwo, Kuti 
Mulungu adzawalipira Malipiro 
abwino pazomwe adali kuchita. 

122.Nkosafunika kwa Asilamu 
kutuluka Onse (m'midzi yawo 
kupita ku Madina ndi kusiya midzi 
yopanda Anthu). Nchifukwa ninji 
Silituluka gulu m'fuko lililonse 
Mwa iwo (ndikupita ku Madina 
kwa Mtumiki) kukaphunzira 
bwino za Chipembedzo, ndipo 
akawachenjeze Anthu awo 
akazabwerera kwa iwo kuti aope. 

123. E inuamene 
mwakhulupirira! Menyani 
nkhondo ndi awo osakhulupirira 
Amene ali pafupi nanu, ndipo 
apeze kuuma (Mtima) mwa inu. 
Ndipo dziwani kuti ndithu 
Mulungu ali pamodzi ndi oopa 
(lye). 

124. Ndipo nthawi zonse sura 
(yatsopano) Ikavumbulutsidwa, 
alipo mwa iwo (Amunafikina) 
amene akunena: "Ndani mwa inu 















Siirat 9. At-Taubah Juzu 11 I 425 I \ > *> 



^ hyd\ Sjj-j 



sura lyi yamuonjezera 
Chikhulupiriro?" Koma amene 
Akhulupirira yawaonjezera 
Chikhulupiriro ndipo iwo 
akukondwera. 

125. Koma amene ali ndi 
matenda m'mitima Mwawo, 
yawaonjezera zoipa Pamwamba 
pazoipa zomwe adali nazo, Ndipo 
akufa ali osakhulupirira. 

126. Kodi saona kuti iwo 
akuyesedwa Mayeso chaka 
chilichonse kamodzi, Kapena 
kawiri, (kapena kochulukirapo)? 
Koma salapa (kwa Mulungu) 
ndiponso Iwo sakumbukira. 

127. Ndipo nthawi iliyonse sura 
yatsopano Ikavumbulutsidwa 
amayang'anana (Iwo amunafikina 
kuti Athawe, asamvere mawu ake, 
uku Akuuzana pakati pawo): 
"Kodi alipo Amene akukuonani?" 
Kenako Amatembenuka 
nkuthawa. Tero, Mulungu 
waikhotetsa Mitima yawo 
chifukwa chakuti iwo ndi Anthu 
osazindikira. 

128. Ndithu, wakudzerani 
Mtumiki Wochokera mwa inu. 
Zikumudandaulitsa lye zomwe 
zikukuvutitsani; lye ngoikira 
mtima pa inu Pokufunirani 
zabwino; Ndipo pa okhulupirira 
Ngodekha ndiponso ngwachisoni. 






\*1 



%%&jyj± 






Surat 9. At-Taubah Juzu 11 



426 



\\ *jJH 



^ 4jjsil Qjj-> 



129. Koma ngati (iwo) apitiriza 
Kunyoza (awo osakhulupirira), 
Nena: "Mulungu wandikwanira 
(Palibe vuto lingapezeke 
Kuchokera kwa inu) palibe Woti 
nkupembedzedwa Koma lye basi. 
Ndatsamira Kwa lye. Ndipo lye, 
ndi Bwana wa Mpando waukulu!" 







Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



427 



U *>» 



^ ♦ a^y- 5 j>* 




SURAT YUNUS X 




Yayamba ndikufotokoza za ulemelero wa Buku la Qur'an ndi 
zomwe Amshirikina ankamunenera Mtumiki Muhammad 
(SAW). Kenako yafotokoza za dziko ndi zisonyezo za Mulungu 
zomwe zili m'menemo zosonyeza kukhoza kwake. 

Surayi yakambanso za mphoto ya tsiku lomaliza (tsiku la 
Kiyama) ndi machitidwe a Mulungu kwa osakhulupirira. Ndipo 
yafotokozanso za chikhalidwe cha anthu pamavuto ndi 
pamtendere. Yakambanso kuti Mulungu ndiye ali ndi mphamvu 
pachilichonse, osati mafano. Ndipo yawatokosa amene akuti 
Qur'an njopeka kuti apeke sura imodzi yonga ngati ya 
m'Qur'an. 

Msurayi Mulungu akuchenjezanso anthu za chilango Chake 
choopsa, ndi momwe mitima ya anthu ilili. Ndipo yanenetsa kuti 
Mulungu akuona chilichonse chimene anthu akuchita. 

Kenako yafotokoza mawu omutonthoza Mtumiki 
pakuwawidwa kwake ndi kusakhulupirira kwa anthu ake pomwe 
adali kuwauza momveka bwino. Ndipo yamthonthoza potchula 
zomwe aneneri ankapezana nazo kwa anthu awo. Choncho 
yadza nkhani ya Nuhi,nkhani ya Musa ndi Haarun pamodzi ndi 
Farawo ndi ana a Israeli. Ndipo kenako yanena nkhani ya Yunus 
yemwe Surayi idatchulidwa ndi dzina lake. 




Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



428 



\ \ *>i 



iT*?- d J>" 



Surat Yunus X 



M'dzina la Mulungu Wachifundo 
Chambih Wachisoni. 

l.Alif-Ldm-Rd. Izi ndi aya za 
m'Buku lanzeru. (Lokamba 
zanzeru zokhazokha). 

2. Kodi nchodabwitsa kwa 
anthu kuti Tamuvumbulutsira 
(chivumbulutso) Munthu wa 
mwaiwo (yemwe ndi 
Muhammad{SAW}) kuti 
achenjeze anthu Ndipowauza 
nkhani yabwino Amene 
akhulupirira kuti iwo adzapeza 
Ulemelero waukulu kwa Mbuye 
Wawo? Osakhulupirira adati: 
"Ndithudi uyu ndi wa Matsenga 
(mfiti) wowonekera". 1 

3. Ndithu, Mbuye wanu ndi 
Mulungu Amene adalenga thambo 
ndi nthaka (Ndi zonse za 
m'menemo) m'masiku Asanu ndi 
limodzi; (masiku omwe Palibe 
yemwe akuwadziwa kutalika 
Kwake koma lye yekha), kenako 
Adakhazikika pampando Wake 
Wachifumu (kukhazikika kwake 
Akukudziwa ndi lye yekha basi), 






;'-.*V 



o^t^t^u- 



— Vtf 



*£M&0& 






L * 9 7 1711 \\ m9 ^ •• 9 ^ * 



<&i%M& 






Mulungu akuti, "Sikunayenere kwa anthu kudabwa ndi kutsutsa 
chivumbulutso chathu kwa munthu wochokera mwa iwo yemwe cholinga 
chake nkuti achenjeze anthu za chilango cha Mulungu ndi kuti awauze nkhani 
zabwino amene mwa iwo akhulupirira. Ndiponso nkosayenera kwa iwo 
kumunenera Muhammadi (SAW), Mtumiki wathu, kuti iye ndi wa matsenga". 



Surat 10. Yiinus 



Juzu 11 



429 



U fr>i 



^ * <j^>3l 5 jJ-*» 



Amayendetsa zinthu (za 
Zolengedwa Zake.) Palibe 
Muomboli (woombola wina) koma 
Pambuyo pa chilolezo Chake 
(Mulungu). Uyo ndiye Mulungu 
Mbuye wanu; choncho 
mupembedzeni lye. Kodi 
simungakumbukire (Kuti 
mafanowo si milungu)? 

4. Kobwerera kwanu nonsenu 
ndi kwa lye. Hi ndilonjezo la 
Mulungu Loona. Ndithu, lye ndi 
Yemwe Adayamba kulenga 
(zolengedwa), ndiponso Ndi 
Yemwe adzazibwereza (pambuyo 
Pa imfa) kuti adzawalipire amene 
Adakhulupirira ndi kumachita 
Zabwino mwa chilungamo. Ndipo 
Amene sadakhulupirire, akapeza 
Zakumwa za madzi owira ndi 
chilango Chopweteka chifukwa 
cha Kusakhulupirira kwawo. 

5. lye (Mulungu) ndi Yemwe 
adapanga Dzuwa kukhala lowala, 
ndi mwezi Kukhala wounika; 
ndipo adaukonzera Mbuto 
(masitesheni ) kuti Mudziwe 
kuchuluka kwa zaka ndi 
Chiwerengero chake. Mulungu 
Sadalenge zimenezo koma 
Mwachoonadi (ndi cholinga cha 
nzeru). Akufotokoza aya (Zake) 
kwa anthu Ozindikira. 1 









Mbuye wanu ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka. Ndipo dzuwa 
adalipanga kuti lizipereka kuwala ku zolengedwa; naonso mwezi kuti 



Siirat 10. Yunus 



Juzu 11 



430 



\\ *jir\ 



^ * j^Ji *Jf 



6. Ndithu, m'kusinthanasinthana 
Kwa (nthawi zonse,) usiku ndi 
Usana ndi zomwe Mulungu walenga 
Kumwamba ndi pansi, ndithudi, 
ndi Zisonyezo kwa anthu oopa. 

7. Ndithu, amene saopa 
kukumana Nafe, Nakondetsetsa 
umoyo wapadziko Lapansi ndi 
kukhazikika (mtima) Ndi za 
mmenemo, ndi omwe akunyozera 
Aya Zathu, 

8. Iwowo (onse) malo awo ndi 
kumoto Chifukwa cha zomwe 
adazipeza (M'njira zosayenera). 

9. Ndithu amene akhulupirira 
ndi Kumachita zabwino,Mbuye 
wawo Awaongola chifukwa cha 
Chikhulupiriro cha wo; (adzalowa 
m'minda Yamtendere) pansi ndi 
Patsogolo pake mitsinje ikuyenda 
M'minda yamtendere. 

10. Mapemphero awo 
m'menemo adzakhala Kunena: 
"'SubuhanakaLahuma' Ulemerero 
ndi wanu, O! Inu Ambuye 
Mulungu!" Ndipo kulonjerana 
Kwawo m'menemo kudzakhala 
kunena: "'Salaam (alayikum') 
Mtendere ukhale painu." Ndipo 















uzitumiza kuunika. Ndipo mwezi adaupangira njira momwe umayenda. Ndipo 
kuunika kwake kumakhala kosiyanasiyana chifukwa cha masitesheniwa. Izi 
nkuti zikuthangateni powerengera nthawi, ndikuti mudziwe chiwerengero cha 
zaka. Mulungu adalenga zimenezi ncholinga chanzeru zakuya. 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



431 



\ > *>» 



^ * cT'Ji 5 JJ~" 



duwa yawo yomaliza (idzakhala 

kuyamika Ponena kuti) " 

' Alham'du Lillah Rabil a'lamin'. 

Kuyamikidwa konse Nkwa 

Mulungu Mbuyewa 

zolengedwa." 1 

1 1 . Ndipo Mulungu akadakhala 
kuti akuwapatsa Anthu zoipa 
mwachangu (zomwe iwo 
akuzifulumizitsa) monga momwe 
iwo Amafulumizitsira (kupeza) 
zabwino (Ndiye kuti) 
ikadalamulidwa nthawi yawo 

( Yowaonongera koma Mulungu 
amawamvera Chisoni) koma 
amene saopa kukumana Nafe, 
Tikuwasiya akuyumbayumba 
m'zoipa Zawo. 

12. Ndipo vuto likamkhuza 
munthu Amatipempha 
(m'kakhalidwe kake Konse), 
chogona, chokhala kapena 
Choimirira. Koma tikamchotsera 
Vuto lomwe lidampeza, amayenda 
ngati Sanatipempheko pa vuto 
lomwe lidamkhudza Momwemo 
ndimo Zakometseredwa kwa 
opyola Malire zomwe ankachita. 












Pemphero la okhulupirira lidzakhaia kumuyeretsa Mulungu kuzimene adali 
kumunenera osakhulupirira pa dziko lapansi. Nayenso Mulungu adzakhala 
akuwalonjera. Ndipo nawo adzakhala akulonjerananso wina ndi mnzake. Uku 
nkutsimikizira mtendere ndi kukhazikika kopanda kutekeseka ndi china 
chilichonse. Ndipo nthawi zonse kothera kwa mapemphero awo ndi kuthokoza 
Mulungu powalimbikitsa pachikhulupiriro. 

2 Munthu vuto likamkhudza mthupi mwake, kapena pachuma chake ndi 
mwina motero apo mpomwe amazindikira za kufooka kwake. Amayamba 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



432 



1 \ *>i 



\ * u~jy~ *jy 



13. Ndipo ndithu, tidaiononga 
mibadwo Yambiri patsogolo panu 
pamene Idachita zoipa. Komatu 
atumiki Awo adawadzera ndi 
zisonyezo Zoonekera, koma sadali 
oti nkukhulupirira. Umo ndi 
momwenso tidzawalipirire Anthu 
ochita zoipa! 

14. Kenako takupangani inu 
(Asilamu) Kukhala olowa m'malo 
mwawo Padziko pambuyo pawo 
kuti tione mmene Mungachitire 
(zabwino kapena zoipa). 

15. Ndipo ay a zathu zomveka 
bwino zikawerengedwa Kwa iwo, 
akunena amene saopa Kukumana 
ndi Ife, "Bwera ndi Qur'an 
(Yogwirizana ndi zofuna zathu) 
osati Iyi, kapena uyisinthe 
(pang'ono)." Nena: "Nkosatheka 
kwa ine kuisintha mwachifuniro 
Changa. Sinditsata koma zimene 
Zikuvumbulutsidwa kwa ine. 
Ndithu, Ine ndikuopa chilango cha 
tsiku lalikulu Ngati ndinyoza 
Mbuye wanga." 

16. Nena: " Mulungu akadafuna, 
Sindikadakuwerengerani Qur'aniyi 












%&%fati&$& 



kumkuwira Mbuye wake Mulungu ndi kumpempha 'kakhalidwe kake konse- 
chogona, chokhala, choimirira kuti amchotsere mliri umene wamgwera. Koma 
Mulungu akamuyankha namchotsera vutolo amamfulatira Mulungu napitiriza 
kumlakwira naiwala ubwino wa Mulungu ngati kuti vuto silidamkhudze, ngati 
kutinso Mulungu sadampemphe konse. ichi ndicho chikhalidwe cha anthu 
ambiri.Amadziwa Mulungu pomwe mavuto akawagwera. Koma akakhala 
pamtendere Mulungu amamuiwala. 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



433 



\\ *>i 



^ • O^Ji ~ JJ** 



Ndiponso sakadakudziwitsani 
Qur'aniyo Ndidakhala pakati panu 
moyo wanga (zaka Zambiri) 
isadavumbulutsidwe 
(Simudandimve ndikunena 
chilichonse Cha utumiki). Kodi 
mulibe nzeru?" 

17. Ndani woipitsitsa woposa 
yemwe Akumpekera Mulungu 
bodza,ndi yemwe Akutsutsa aya 
Zake? Ndithudi, Sangapambane 
wochita zoipa. 

18.Ndipo iwo akupembedza 
milungu yina kusiya Mulungu, 
yomwe singathe kuwapatsa 
masautso (Ngati atasiya 
kuipembedza) ndiponso Siyingathe 
kuwapatsa chithandizo (ngati 
Atalimbika kuipembedza) ndipo 
akunena:"Iwo (Mafanowo) ndi 
aomboli athu kwa Mulungu". 
Nena: "Kodi mukumuuza 
Mulungu zomwe sakudziwa 
Kumwamba ndi pansi? 
Wapatukana Mulungu Ndipo 
watukuka kuzimene 
akum'phatikiza nazo. 

19. Ndipo ndithudi anthu kalero 
(M'nthawi ya Adam) adali mpingo 
Umodzi (opembedza Mulungu 
M'modzi), Koma adasiyana 
(pambuyo pake). Ndipo 
pakadapanda liwu lochokera Kwa 
Mbuye wako, lomwe lidatsogola 
(Lakuti adzawalanga tsiku la 









©(•y^P^I 









Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



434 



n *>» 



y * a^¥- 5 JJ-" 



Kiyama), Ndithu, 
kukadaweruzidwa pakati pawo 
M'zomwe adali kusiyana. 1 

20.Ndipo akunena: "Bwanji 
sichidatsitsidwe Kwa iye 
chizindikiro (chotsimikizira 
Uneneri wake) chochokera Kwa 
Mbuye wake (chomwe takhala 
Tikuchipempha nthawi ndi 
nthawi?") Nena (kwa i wo): 
"Ndithu, kudziwa Zobisika nkwa 
Mulungu yekha. Choncho dikirani 
(chiweruzo cha Mulungu) inenso 
pamodzi nanu ndine Mmodzi wa 
odikira". 

21. Ndipo tikawalawitsa anthu 
Mtendere pambuyo pa masautso 
omwe Adawakhudza, pompo iwo 
amayamba Kuzichitira ndale aya 
Zathu. Nena: "Mulungu 
ngwachangu kwambiri Poononga 
ndale (zawo)" Ndithu, Amithenga 
athu (Angelo) akulemba Ziwembu 
zanu (zonse) zimene mukuchita. 

22. Iye ndi Yemwe 
amakuyendetsani Pamtunda ndi 
panyanja; kufikira Pom we 









aj^^oSSIM» 



9 9 S9" 'XL 



Ndithudi, anthu mchilengedwe chawo adali a mpingo umodzi wogonjera 
Mulungu mwa chilengedwe. Kenako Mulungu adawatumizira aneneri kuti 
awatsogolere kunjira Yake molingana ndi chilamulo chake Mulungu. Koma 
ngakhale zili tere anthu adali ndi ufulu mwa chilengedwe chawo kulandira 
choipa kapena chabwino. Potero, choipa chidawagonjetsa ena a iwo natsata 
zilakolako za satana.nasiyana ndi anzawo chifukwa chazimenezo. Komatu 
padali lamulo la Mulungu la pachiyambi loti oipa sadzawalanga mwachangu 
koma kufikira nthawi yawo itakwana. Pakadapanda lamuloli ndiye kuti onse 
akadawalanga nthawi yomweyo. 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



435 



n *>i 



^ * tHji 5 JJ~* 



mumakhala m'zombo; ndipo 
Zimayenda nawo (zombozo) ndi 
Mphepo yabwino, naisangalalira. 
(Mwadzidzidzi) namondwe 
Nkuzidzera (zombozo) ndipo 
Mafunde nkuwadzera mbali zonse 
Natsimikiza kuti azingidwa (ndi 
Chionongeko); amampempha 
Mulungu modzipereka Kwa lye 
mukupempha kwawo (uku 
Akunena): "Ngati mutipulumutsa 
Pa ichi, tidzakhala m'gulu la 
Oyamika (nthawi zonse)!" 

23. Koma akawapulumutsa, 
pompo akuyamba Kudzitukumula 
ndi kuononga padziko Popanda 
chowayenereza (kutero). E inu 
anthu! Kuononga kwanu 
Kukubweretserani masautso inu 
Nokha. Ndipo chisangalalo (chake) 
Chamoyo wadziko lapansi 
(nchochepa). Kenako kobwerera 
kwanu ndi kwa Ife, Ndipo 
tidzakuuzani zomwe munkachita. 

24. Ndithu, fanizo la moyo 
wadziko Lapansi lili ngati madzi 
amvula Tawatsitsa kuchokera 
kumitambo nkusakanikirana Ndi 
zomera zam'nthaka zomwe Anthu 
ndi nyama amadya; kufikira 
Nthaka ikakwaniritsa kukongola 
Kwake ndi kudzikometsa ndipo eni 
(Nthaka) nkuganiza kuti iwo ali 
Ndi mphamvu panthakayo 
(pokolola Zomwe zili pamenepo). 



O-oJ 















Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



436 



U *>» 



^ • j~*ji *jj-» 



Mwadzidzidzi Nkuzidzera lamulo 
Lathu (zapanthakazo), Usiku 
kapena masana, nkuzichita 
Kukhala ngati zokololedwa ngati 
Kuti sizidalipo dzulo (lake). 
Motere tikufotokoza aya kwa 
anthu Olingalira. 

25. Ndipo Mulungu akuitanira 
(anthu Ake) kunyumba 
yamtendere.Ndipo 
Amamuongolera kunjira yolunjika 
Amene wamfuna (ngati ali 
wotheka Kuongoka). 

26. Ndipo omwe achita 
zabwino, adzapata (Malipiro) 
abwino ndi zoonjezera. Ndipo 
fumbi silikavindikira nkhope 
Zawo. Ndiponso kunyozeka 
Sikukawapeza. Iwowo ndiwo 
anthu A ku Munda wa Mtendere; 
mmenemo Akakhala muyaya. 

27. Ndipo amene akolola zoipa 
(kuchokera M'zochita zawo zoipa) 
mphoto ya Choipa ndiyofanana ndi 
icho; Ndipo kunyozeka 
kudzawapeza; Sadzakhala ndi 
aliyense wotha Kuwateteza 
kuchilango cha Mulungu. Nkhope 
zawo zidzakhala ngati 
Zaphimbidwa ndi zidutswa za 
Usiku wa m'dima, (zidzakhala 
Zakuda kwambiri); awo ndiwo 
anthu Akumoto. I wo mmenemo 
adzakhala Muyaya. 



%;mm 









GQ\\LK\'-L 






Siirat 10. Yunus 



Juzu 11 



437 



>\ *>i 



^ * U^Ji 5 JJ~" 



28. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
lomwe Tidzawasonkhanitsa onse. 
Kenako Tidzawauza amene 
ankaphatikiza Mulungu (kuti): 
"Imani pompo inu Pamodzi ndi 
aphatikizi anuwo". Ndipo 
tidzawasiyanitsa pakati pawo; 
Koma aphatikizi awowo adzati: 
"Simudali kutipembedza ife 
(Koma mudali kupembedza 
Zilakolako zanu). 

29. "Mulungu akukwanira 
kukhala mboni Pakati pathu ndi 
pakati panu. Ndithu, ife sitidali 
kuzindikira Za mapemphero anu. 
(Sitinkazindikira Kuti inu 
mukutipembedza)" 

30. Kumeneko munthu aliyense 
adzadziwa Zimene adatsogoza; 
ndipo adzabwezedwa Kwa 
Mulungu, Mbuye wawo Woona 
Ndipo zidzawasowa zimene adali 
Kupeka. 

31.Nena: "Kodi ndani 
akukupatsani (Zopatsa) kuchokera 
kumwamba (Povumbwitsa mvula), 
ndi pansi (Pomeretsa mmera)? 
Nanga Ndani amakupatsani kumva 
ndi Kupenya? Nanga ndani amene 
Akutulutsa chamoyo kuchokera 
m'chakufa, Ndi kutulutsa chakufa 
m'chamoyo? Nanga ndani 
akukonza zinthu zonse?" Anena: 
"Ndi Mulungu." Choncho, Nena: 
"Kodi bwanji Simukumuopa?" 












Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



438 1 > *>* 



\ • cT^Ji ^J" - 



32. Uyo ndi Mulungu, Mbuye 
wanu Woona; Nanga pali chiyani 
Pambuyo poleka choonadi, 
Sikusokera basi? Kodi nanga 
Mukutembenuzidwa chotani 
(kusiya Choonadi)? 

33. Momwemo liwu la Mbuye 
wako Latsimikizika kwa amene 
Adatuluka m'chilamulo cha 
Mulungu kuti iwo 
sadzakhulupirira. 

34. Nena: "Kodi alipo mwa 
amene Mukuwaphatikiza ndi 
Mulungu Amene angayambitse 
kulenga Zolengedwa; kenako 
(Zitafa) ndikuzibweza?" Nena: 
"Mulungu ndi Yemwe 
akuyambitsa Zolengedwa kenaka 
ndi kuzibweza (Pambuyo 
poonongeka). Nanga 
mukutembenuzidwa chotani 
(Kusiya chikhulupiriro)? 

35. Nena: "Kodi alipo mwa 
amene Mukuwaphatikiza ndi 
Mulungu, Woongolera 
kuchoonadi?" Nena: "Mulungu ndi 
Yemwe Akuongolera kuchoonadi. 
Kodi Amene akutsogolera 
kuchoonadi Sindiye woyenera 
kwambiri Kutsatidwa kapena 
(woyenera Kutsatidwa ndi) yemwe 
sakutha Kudziongola pokhapokha 
atawongoledwa ndi Wina wake? 
Nanga mwatani kodi? 
Mukuweruza 






*- "-&$&$ 












eQff'"* 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



439 



\\ *>! 



^ * U^Ji 5 JJ"*' 



36. Ndipo ambiri a iwo satsatira 
(China) koma zoganizira basi, 
(Osati chomwe afufuza 
ndikuchizindikira Ndi nzeru 
zawo). Ndithu Choganizira 
sichithandiza Ngakhale pang'ono 
ku Choonadi. Ndithu, Mulungu 
akudziwa Zonse zimene akuchita. 

37. Ndipo sikotheka Qur'an iyi 
Kukhala yopekedwa, yosachokera 
Kwa Mulungu (monga momwe 
Munenera). Koma (yachokera Kwa 
Mulungu) kutsimikizira Zomwe 
zidalipo patsogolo pake, Ndi 
kulongosola za Mabuku (Akale). 
Palibe chikaiko m'menemo (Kuti) 
yachokera kwa Mbuye wa 
Zolengedwa. 

38. Kapena akunena kuti 
waipeka? Nena: "Tabwerani ndi 
Sura (imodzi) Yofanana ndi iyo, 
ndipo itanani Amene mungathe 
(kuwaitana kuti Akuthandizeni) 
kupatula Mulungu, Ngati inu 
mukunena zoona (kuti Qur'aniyi 
waipeka Muhammad {SAW})." 

39. Koma atsutsa zomwe 
sakuzizindikira (M'mene zilili) 
ngakhale tanthauzo lake (Lakuona 
kwake kapena kunama kwake) 
Lisanawafikebe. Momwemonso 
adatsutsa Omwe adalipo patsogolo 
pawo. Choncho, taona momwe 
mathero A anthu ochimwa adalili. 















Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



440 



U frjJrl 



^ * jr^3i 5 jJ-*» 



40. Ndipo mwa iwo pali ena 
omwe Akuikhulupirira (Qur'an), 
ndipo ena mwa iwo 
Sakuikhulupirira. Ndipo Mbuye 
Wako akuwadziwa bwino 
oononga. 

4 1. Ndipo ngati apitiriza 
kukutsutsa, nena: "Ine ndiri ndi 
ntchito yangajnunso muli ndi 
ntchito yanu. Inu mwatalikirana 
nazo zimene Ndikuchita, inenso 
ndatalikirana nazo Zimene 
mukuchita!" 

42. Ndipo mwa iwo alipo ena 
amene akumvetsera Kwa iwe, 
(koma osati ndi Cholinga choti 
adziwe). Kodi Iwe ungathe 
kuwamveretsa agonthi, 
Chikhalirecho nzeru alibe? 

43. Ndipo alipo ena mwa iwo 
Amene akukutong'olera Maso 
(kukuyang'ana Monyoza). Kodi 
iwe ungathe Kuwatsogolera 
akhungu, Chikhalirecho sali 
openya? 

44. Ndithu, Mulungu sachitira 
anthu Choipa chilichonse. Koma 
anthu Akudzichitira okha zoipa. 
(Adapatsidwa nzeru, koma 
Sazigwiritsa ntchito). 

45. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
lomwe Adzawasonkhanitsa (onse) 
ngati Kuti sadakhale (padziko 
lapansi) Koma ola limodzi la usana 















S9.&' ' 9 £9?'" ' 9K"\*" \'^\\ 



Siirat 10. Yunus 



Juzu 11 



441 



\\ *>i 



L^y 'm-* 



(Atathedwa nzeru). 
Adzazindikirana Pakati pawo; 
(koma aliyense Sadzalabadira 
mnzake). Ndithu, Aonongeka 
amene adatsutsa za Kukumana ndi 
Mulungu Ndipo sadali oongoka. 

46. Ndipo ngati tingakusonyeze 
(pompano Padziko lapansi) zina 
mwa Zomwe tikuwalonjeza 
ndikuwachenjeza Nazo, kapena 
kukubweretsera Imfa (usadazione 
zimenezo), Kobwerera kwawo 
nkwa Ife basi. Kenako Mulungu 
ndi mboni pa Zomwe akuchita. 

47. Ndipo fuko lililonse lili ndi 
Mtumiki Ndipo akazabwera 
Mtumiki Wawo (tsiku la 
chiweruzo) Kudzaweruzidwa 
pakati Pawo mwachilungamo 
Ndipo sadzaponderezedwa. 

48. Ndipo akunena 
(osakhulupirira): "Kodi Lonjezo ili 
lidzachitika liti Ngati mukunena 
zoona?" 

49. Nena: "Ndilibe mphamvu 
mwandekha pa (Kudzichotsera) 
vuto ngakhale (Kudzibweretsera) 
thandizo. (Nanga za zimenezo 
ndingadziweponji)? Koma 
chimene Mulungu wafuna (ndi 
Chomwe chimachitika). M 5 bad wo 
uli Wonse uli ndi nthawi yake 
(yofera). Nthawi yawo (yofera) 
ikadza Sangathe kuichedwera ola 
limodzi Ngakhale kufulumira." 



«^0^Ai$yST 



&&<jc$\J%&j% 



a#a&*r«K&2 















Surat 10. Yiinus 



Juzu 11 



442 



\\ *>! 



^ * cHji 5 J>" 



50. Nena: "Kodi mukuona 
bwanji, ngati Chilango Chakecho 
chitakudzerani Usiku kapena usana 
(mungathe Kuthawa)? Nanga 
bwanji ochimwa 
Akuchifulumizitsa (kuti chidze 
Mwachangu)? 

51. "Kodi chikadza ndi pamene 
Mudzachikhulupirire?" 
(Panthawiyo mudzauzidwa): "Kodi 
tsopano (ndi pamene 
Mukukhulupirira), chikhalirecho 
Mudali kuchifulumizitsa (kale)?" 

52. Kenako kudzanenedwa kwa 
amene Adachita zoipa: "Lawani 
chilango Chamuyaya! Kodi 
mungalipidwe Zina osakhala 
zomwe mudazipata (kuchokera 
m'zochita zanu Zoipa)!" 

53. Eti akukufunsa: "Kodi 
nzoona Izo (zimene ukunena)?" 
Nena: "Inde! ndikulumbira kwa 
Mbuye Wanga, zimenezo ndi 
zoona. Ndipo inu simungathe 
kulepheretsa (Mulungu)." 

54. Ndipo kukadakhala kuti 
munthu Aliyense amene adachita 
zoipa, Nkukhala nazo zonse 
zam'dziko Akadapereka zonse kuti 
adziombole Nazo (pamene 
adzaona kuopsa kwa Chilango cha 
tsikulo). Ndipo Akadzachiona 
chilango, adzayesetsa Kubisa 
madandaulo (awo; koma 


















Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



443 



U *>» 



^ * cT^Ji 5 JJ-° 



Adzaonekera poyera).Ndipo 
kudzaweruzidwa Mwachilungamo 
pakati pawo, ndipo Iwo 
sadzaponderezedwa. 

55. Tamverani! Ndithu, zonse 
Zakumwamba ndipansi nza 
Mulungu. Tamverani! Ndithu, 
lonjezo la Mulungu ndi loona. 
Koma ambiri a Iwo sadziwa. 

56. lye (Mulungu ndi amene) 
amapereka Moyo ndi imfa. Ndipo 
kwa lye (Nonsenu) 
mudzabwezedwa. 

57. E inu anthuINdithu, ulaliki 
Wakudzerani kuchokera kwa 
Mbuye Wanu ndi chochiritsa 
zomwe (matenda) Zili m'mitima 
mwanu, Ndiponso nchiongoko ndi 
chifundo Kwa okhulupirira. 

58. Nena: "Chifukwa cha 
ubwino wa Mulungu ndi chifundo 
Chake, (Mwapeza zimenezi), 
choncho Asangalalire zimenezi." 
Izi Ndizabwino kwambiri kuposa 
Zimene akusonkhanitsa (m'zinthu 
Za dziko lapansi). 

59. Nena: "Kodi mukuona 
bwanji, Riziki lomwe Mulungu 
wakutsitsirani? Kenako inu Una 
mwa ilo mwalichita kukhala 
Loletsedwa (la haramu), ndipo 
lina mwa ilo Kukhala lololedwa (la 
halali)." Nena: "Kodi Mulungu 
adakulolezani (Kuchita zimenezo), 















s^'it*-' 









Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



444 



U *j*-i 



U^3i d Ji- 



kapena mukumpekera Mulungu 
bodza?" 

60. Kodi ali ndi ganizo lotani 
amene Akumpekera Mulungu 
bodza pa za Tsiku la Kiyama? 
Ndithu, Mulungu Ndi Mwini 
ubwino wochuluka kwa Anthu. 
Koma ambiri aiwo Sathokoza. 

61.Ndipo siutanganidwa ndi 
ntchito Iliyonse, ndiponso 
simuwerenga M'menemo (chinthu 
chilichonse) Cha m'Qur'an ndipo 
simuchita Ntchito ina iliyonse (inu 
anthu) Koma Ife timakhala mboni 
pa Inu pamene mukutanganidwa 
nayo. Ndipo sichibisika kwa 
Mbuye Wako chinthu chilichonse 
ngakhale Cholemera ngati nyerere, 
m'nthaka Ngakhale kumwamba. 
Ndipo ngakhale Chocheperapo 
zedi kuposa pamenepo Kapena 
chokulirapo koma chili M'Buku 
(la Mulungu) lofotokoza 
Chilichonse. 

62. Tamverani! Ndithu, 
okondedwa A Mulungu sadzakhala 
ndi mantha (Pa tsiku la 
Kiyama),ndipo Sadzadandaula; 

63. (Amenewo ndi) amene 
Adakhulupirira Ndi kumuopa 
Mulungu; 

64. Iwo ali ndi zabwino pamoyo 
wadziko Lapansi ndi pa tsiku 
lomaliza. Palibe kusintha pa mawu 









® 



T V A<V. 






Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



445 



\\ *>i 



LT^y- °jj^ 



a Mulungu. Uku ndiko kupambana 
Kwakukulu. 

65. Ndipo (iwe, 
Mtumiki{SAW}) 
Zisakudandaulitse zonena zawo 
(zomwe Akukunenera monyoza). 
Ndithu, ulemerero Ndi mphamvu 
zonse nza Mulungu. lye 
Ngwakumva, Ngodziwa. 

66. Tamverani! Ndithu,(zonse) 
Zakumwamba ndi zapansi, nza 
Mulungu. Ndipo amene 
akupembedza Zina kusiya 
Mulungu, Satsatira aphatikizi (a 
Mulungu), Akungotsatira 
zoganizira. Ndipo iwo sanena 
china Koma bodza basi. 

67. lye (Mulungu) ndi Yemwe 
adakupangirani Usiku kuti 
muzipumamo. Ndipo 
(adakupangirani) usana kukhala 
Wowala (kuti mupenye). Ndithu, 
M'zimenezo muli zisonyezo 
(Zosonyeza chifundo cha Mulungu 
Pazolengedwa Zake) kwa anthu 
Akumva. 

68. Akunena: "Mulungu 
wadzipangira Mwana" wapatukana 
ndi zimenezo! lye Ngokwanira, 
(Salakalaka Mwana ngakhale 
mthangati aliyense). Ndi zake 
(zonse) zakumwamba ndi zapansi. 
Inu mulibe umboni pazimenezi. 
Kodi Mukumnenera Mulungu 
zomwe Simukuzidzidwa? 



kfl&fSk 



© 















Surat 10. Yiinus 



Juzu 11 



446 



n *>i 



LT'Ji *JJ" 



69. Nena: "Ndithu, amene 
Akumpekera Mulungu Bodza, 
sadzapambana". 

70. Ndichisangalalo chochepa 
basi M'dziko lapansi.Kenako kwa 
Ife ndiwo mabwerero awo. Kenako 
tidzawalawitsa chilango Chaukali 
chifukwa cha kusakhulupirira 
Kwawo. 

71. Ndipo awerengere 
(molakatula) nkhani za Nuhi 
pamene adanena kwa anthu ake, 
"E inu anthu anga! Ngati kukhala 
Kwanga pamodzi ndi inu ndi 
Kukumbutsa kwanga aya za 
Mulungu Kukunyansani, ine 
ndatsamira kwa Mulungu 
(sindisiya ntchito yangayi). Inunso 
sonkhanitsani zinthu zanu Pamodzi 
ndi milungu yanuyo; (Sonkhanani 
kuti mundichitire choipa, Ine 
sindilabadira chilichonse). Ndipo 
Chinthu chanucho chisabisike kwa 
inu, (Chitani moonekera. Ine 
sinditekeseka Ndi chilichonse). 
Kenako chitani pa ine (Chimene 
mufuna kuchita) ndipo 
Musandipatse danga. 

72. Ngati mutembenuka ndi 
kunyoza, (Ndikufuna kwanu).Ine 
sindinakupempheni Malipiro . 
Malipiro anga kulibe Kulikonse 
(kumene ndingalandire) Koma 
kwa Mulungu, ndipo 









®&££\ 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



447 



U *>) 



\ ♦ j-Jji 5jj-» 



Ndalamulidwa kuti ndikhale 
Mmodzi wa ogonjera lye". 

73. Koma adamutsutsa. 
Choncho Tidampulumutsa 
pamodzi ndi Amene adali naye 
m'chombo. Ndipo tidawasankha 
iwo kukhala Otsala (padziko 
anzawo ataonongeka). Ndipo 
tidawamiza amene adatsutsa aya 
Zathu. Taona momwe mapeto A 
ochenjezedwa adalili! 

74. Pambuyo pake tidawatumiza 
Atumiki Ambiri kwa anthu awo. 
Adawadzera Ndi mitsutso 
(zisonyezo) yoonekera Poyera 
koma sadali okhulupirira zimene 
Ena adazitsutsa kale,(adatsatira 
Njira zomwezo za anzawo). Umo 
ndi momwe Tikudindira zidindo 
m'mitima ya anthu Opyola malire. 

75. Pambuyo pawo tidamtuma 
Musa ndi Haaruna pamodzi ndi 
zizindikiro zathu kwa Farawo ndi 
nduna zake. Koma adadzikweza. 
Tero adali anthu oipa. 

76. Ndipo pamene choonadi 
chidawadzera Kuchokera kwa Ife, 
adanena: "Ndithu, Awa ndi 
matsenga oonekera." 

77. Musa adati: "Mukutero 
pachoonadi Pamene chakudzerani? 
Kodi matsenga ali Chonchi? 
(Bwanji ichi chapambana)? Ndipo 


















Surat 10. Yiinus 



Juzu 11 



448 



n *>■! 



\ « ^pjji «jj~- 



amatsenga sangapambane 
(Ngakhale zitatani)" 

78. (Iwo) adati: "Kodi 
watidzera kuti Utichotse kuzimene 
tidawapeza nazo Makolo athu kuti 
ukulu ukhale wa inu (Awiri) 
mdzikoli? Koma ife 
Sitingakukhulupirireni awirinu." 

79. Ndipo Farawo adati: 
"Ndibweretsereni Wamatsenga 
aliyense wodziwa Kwambiri 
(zamatsenga)." 

80. Ndipo pamene amatsenga 
adadza, Musa adati kwa iwo: 
"Ponyani Zomwe mufuna kuponya 
(Kuti musonyeze ukatswiri Wanu 
kwa anthu)". 

81. Pamene adaponya, Musa 
adati: "Zomwe mwabweretsa ndi 
matsenga. Mulungu awaononga 
pompano. Ndithu, Mulungu 
Sakonza ntchito Za oononga. 

82. Ndipo Mulungu 
achilimbikitsa Choonadi ndi mau 
Ake, ngakhale Oipa anyansidwe 
nazo". 

83. Sadamkhulupirire Musa 
kupatula Anyamata a mwa anthu 
ake, chifukwa Choopa Farawo ndi 
nduna zake kuti Angawazunze. 
Ndithu, Farawo adali Wodzikuza 
padziko, ndithudi, adali M'modzi 
mwa opyola malire. 






a^Q&$I^M@b 









w 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



449 1 1 > *j*-» 



^ * c/^Ji 5 J>^ 



84. Ndipo Musa adati: "E inu 
anthu Anga! Ngati inu 
mwakhulupirira Mulungu, 
choncho tsamirani kwa lye Ngati 
mulidi Asilarnu (oona). 

85. (I wo) adati: "Tayadzarnira 
kwa Mulungu. O Mbuye wathu! 
Musatichite kukhala Ozunzidwa 
ndi anthu oipa. 

86. Ndipo tipulumutseni Mwa 
chifundo Chanu ku anthu 
Osakhulupirira." 

87. Ndipo tidavumbulutsa kwa 
Musa ndi M'bale wake mawu 
Athu (oti): "Apangireni nyumba 
anthu anu mu Eguputo ndipo 
nyumba zanu zichiteni Kukhala 
misikiti (pakuti simungathe 
Kukhala ndi misikiti yoonekera), 
Ndipo pempherani Swala. Ndipo 
auze Nkhani yabwino okhulupirira 
(kuti Mulungu awapatsa zabwino 
pamoyo Wadziko lapansi ndi 
patsiku lomaliza)." 

88. Ndipo Musa adati: "Mbuye 
wathu! Inu mwampatsa Farawo ndi 
nduna zake Zodzikometsera, ndi 
chuma chambirimbiri Pamoyo 
wapadziko. Mbuye wathu, 
Choncho iwo akusokeretsa anthu 
pa Njira yanu. Mbuye wathu, 
wonongani Chuma chawo ndipo 
iumitseni mitima Yawo popeza 
sakhulupirira kufikira Ataona 
chilango chowawa." 



"b 









*%jJH\J&fitf& 



®r,'i3>. 






Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



450 



U *>» 



^ * U^Ji ~ d JJ~* 



89. (Mulungu) adati: "Pempho 
Lanu lavomerezedwa! Choncho 
lungamani Mwaubwino, musatsate 
njira za omwe Sadziwa." 

90. Ndipo tidawaolotsa 
panyanja ana a Israeli. Ndipo 
Farawo ndi asilikali Ake ankhondo 
adawatsata moipitsa ndi 
Mwamtopola, kufikira pamene 
kumira Kudampeza; (iye) adati: 
"Ndakhulupirira Kuti palibe 
wopembedzedwa mwachoonadi 
Koma yemwe ana a Israeli 
amkhulupirira. Ndipo ine ndine 
mmodzi mwa Omugonjera (monga 
iwo akumgonjera)." 

91. (Angelo adamuuza kuti:) 
"Tsopano (Ndi pamene 
ukukhulupirira), pomwe Kale 
udanyoza ndikukhala mmodzi 
Waoononga!" 

92. "Choncho lero 
tikupulumutsa (polisunga) Thupi 
lako, kuti ukhale chisonyezo kwa 
Amene akudza m'mbuyo mwako 
(kuti adziwe Kuti sudali Mulungu). 
Koma ndithu, Anthu ambiri 
salabadira zisonyezo Zathu." 

93. Ndipo (pambuyo pake) 
tidawakonzera Mokhala 
mwabwino ana a Israeli, 
Ndikuwapatsa zabwino. 
Sadasiyane Kufikira pamene nzeru 
zidawadzera. Ndithu, Mbuye wako 






***<a$$Z&$*s 















Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



451 



U frj*-* 



u*y-*jy* 



adzaweruza pakati Pawo tsiku la 
Kiyama pazimene adali 
Kutsutsana. 

94. Ngati uli ndi chipeneko 
pazimene Takuvumbulutsira, 
afunse amene akuwerenga Mabuku 
akale (Ayuda ndi Akhrisitu Amene 
alowa m'Chisilamu). Ndithu, 
Choonadi chakufika kuchokera 
kwa Mbuye wako. Choncho 
usakhale mwa Amene akukaikira. 

95. Ndiponso usakhale mwa 
omwe akutsutsa Zizindikiro za 
Mulungu, kuopa kuti 
Ungadzakhale m'gulu la.otaika. 

96. Ndithu, aja amene liwu la 
Mbuye wako latsimikizika pa iwo, 
Sakhulupirira. 

97. Ndipo ngakhale kuti 
chisonyezo chamtundu Uliwonse 
chiwadzere, mpaka aone Chilango 
chopweteka. 

98. Kodi udalipo mudzi (ndi 
umodzi womwe Pakati pamidzi 
mwa yomwe tidaiwononga), 
Umene udalapa ndi kukhulupirira 
(Pambuyo poona chilango kotero 
kuti) Chikhulupiriro chake 
nkuuthandiza Panthawi imeneyo, 
osati kupatula anthu a Yunus 
okha? (Ndi anthu a Yunus okha 
Amene adakhulupirira pamene 
adazindikira Za chilango kuti 
chikudza. Choncho 






bs 






sua 






Siirat 10. Yunus 



Juzu 11 



452 



U *>l 



^Ji °JJ^ 



Adapulumuka). Pamene 
adakhulupirira, Tidawachotsera 
chilango choyalutsa M'moyo 
wapadziko lapansi, ndipo 
Tidawasangalatsa kufikira nthawi 
yawo (Yofera). 

99. Ndipo Mbuye wako 
akadafuna (kuwakakamiza anthu 
Mwamphamvu kuti akhulupirire), 
onse ali Mdziko lapansi 
akadakhulupirira (Sipakadatsala 
ndi mmodzi yemwe. Koma 
Mulungu safuna kukakamiza anthu 
Mwamphamvu). Nanga kodi iwe 
uwakakamiza Anthu kuti akhale 
okhulupirira. 

100. Ndipo palibe munthu 
angakhulupirire Popanda chilolezo 
cha Mulungu. lye Amaachitira 
ukali amene alibe Nzeru (amene 
sagwiritsa Ntchito nzeru zawo). 

lOl.Nena: "Yang'anani 
nchiyani chikupezeka Kumwamba 
ndi pansi!" Ndipo zisonyezo 
Zonsezi ndi machenjezo onsewa 
Sangawakwanire (ndi 
kuwapindulira Kanthu) anthu 
osakhulupirira. 

102. Kodi chiliponso chimene 
akudikira Osakhala (kuwadzera) 
monga masiku (Azilango zomwe 
zidawapeza) amene Adapita kale 
(iwo asadafike)? Nena: "Dikirani 
nanenso ndili Pamodzi nanu mwa 
odikira." 















% t 



<" L~? 9 fl '* 



b* 



v> 



Surat 10. Yunus 



Juzu 11 



453 I * > *>» 



U**M *Jf 



103. Kenako tidzawapulumutsa 
aneneri Athu ndi amene 
adakhulupirira. Chotere nkoyenera 
kwa Ife kuwapulumutsa 
Okhulupirira. 

104.Nena: "E inu anthu! Ngati 
inu muli Ndi chipeneko pa 
chipembedzo changa, (Dziwani 
kuti) sindingapembedze zimene 
Mukuzipembedza kusiya 
Mulungu; Koma Ine ndipembedza 
Mulungu (Mmodzi yekha) Yemwe 
amakupatsani imfa (ndi moyo). 
Ndipo ndalamulidwa kukhala 
mmodzi wa Okhulupirira, 

lOS.Ndiponso (ndauzidwa 
kuti): 'Lungamitsa nkhope yako 
kuchipembedzo Momuyeretsera 
Mulungu mapemphero Ake, Ndipo 
usakhale mmodzi mwa ophatikiza 
Mulungu ndi zinthu zina; 

106. Ndipo (kuti), usapembedze 
chimene Sichingakupindulitsire 
zabwino, kapena Kukubweretsera 
masautso, kusiya Mulungu. Ngati 
utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi 
Wa oipa." 

107. Ndipo ngati Mulungu 
atakukhudza ndi masautso, Palibe 
aliyense owachotsa kupatula lye. 
Ngatinso atakufunira 
zabwino,palibe Amene 
angaubweze ubwino Wake. (lye) 
Amadza ndi ubwinowo kwa amene 









<% 












Surat 10. Yunus 



Juzu 11 454 > > tjJr 



^ % cT^Ji *Jf 



wamfuna Mwa akapolo Ake. 
Ndipo lye Ngokhululuka 
Ngwachisoni . 

108.Nena:"E inu 
anthuIChoonadi chakudzerani 
Kuchokera kwa Mbuye wanu. 
Choncho amene Waongoka, 
(zabwino zake) zili pa iye mwini. 
Ndipo amene wasokera, ndithu 
zotsatira Zakusokera zili pa iye 
mwini. Ndipo ine Sindili 
muyang'aniri pa inu, (udindo 
wanga Ndi kuchenjeza basi)" 

109. Ndipo (andiuza kuti): 
"Tsatira zimene 
Zikuvumbulutsidwa kwa iwe 
ndipo pirira Kufikira Mulungu 
adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino 
kuposa aweruzi onse." 






«y« 







Suratll.Hud 



Juzu 11 



455 



n *>i 



^ S ijA 5jj**> 



Stoat Hud XI 



* 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Alif-Lam-Ra. Hi ndi buku 
lomwe ndime Zake zakonzedwa 
bwino ndipo zafotokozedwa 
Mwatsatanetsatane kuchokera kwa 
Mulungu Mwini nzeru zakuya 
Wodziwa chilichonse. 

2. (Wachita zimenezi) kuti 
musampembedze wina Wake 
koma Mulungu yekha. Ndithudi 
ine kwa inu Ndi mchenjezi 
wochokera kwa lye ndiponso 
Wokuuzani nkhani zabwino . 

3. Ndikuti mupemphe 
chikhululuko kwa Mbuye wanu 
Ndipo mulape kwa lye. 
Akupatsani chisangalalo Chabwino 
mpakana m'nthawi idaikidwa. 
Ndipo adzampatsa (tsiku 
lachimaliziro) aliyense Wochita za 
ufulu, ufulu wake. Koma, ngati 
Mupotoka ine kwanga 
nkukuoperani za Chilango cha 
tsiku lalikulu. 

4. Kobwerera kwanu nkwa 
Mulungu basi. lye ali Ndi 
mphamvu pa chilichonse. 

5. Tamverani! Iwo akubisa 
zimene zili m'mitima Yawo kuti 
amubise lye (Mulungu). Mverani! 



o^j)t^j)l*kU- 



-^ 


















Su i at 11. 1 hid 



Juzu 12 



456 > t >>> 



> > i^A 6jj~> 



Ndithudi pamene akuzifunda nsalu 
Zawo lye akudziwa zimene 
akuzibisa ndi Zimene akuzionetsa. 
Ndithudi lye ndiwodziwa Za 
mzifuwa. 

6. Ndipo palibe nyama iliyonse 
(cholengedwa Chilichonse) 
panthaka koma riziki lake Lili kwa 
Mulungu; Ndipo (lye) akudziwa 
Mbuto yake yamuyaya ndi mbuto 
yake Yakungodutsapo (yomwe ndi 
pano padziko Lapansi). Zonse zili 
m'buku lofotokoza Chilichonse. 1 

7. Ndipo lye ndi Yemwe 
adalenga Thambo ndi nthaka 
M'masiku asanu ndi limodzi, 
ndipo Mpando Wake wachifumu 
udali Pamadzi. (Adakulengani) 
Kuti akuyeseni mayeso, ndani 
mwa inu ali Wochita zabwino. 
Koma ukanena (kwa Iwo kuti): 
"Inu mudzaukitsidwa pambuyo Pa 
imfa," Amene sadakhulupirire 
akuti, "Izi sikanthu koma ndi 
matsenga oonekera. 2 

8. Ndipo ngati 
titawachedwetsera chilango Mpaka 



ymd$&®g$z 



% 









p\&6a\%&&tys 



Mawu oti "Riziki lake lili kwa Mulungu" nkuti Mulungu wapatsa chilichonse 
mphamvu zofunira riziki lake (zoyendetsa moyo wake). Ndimeyi siitanthauza 
kuti munthu angokhala popanda kugwira ntchito nayembekezera kuti riziki 
lichokera kumwamba. Koma munthu agwire ntchito molimbikira kuti apeze 
chuma cha Mulungu. Zotere nzimene Qur'an ikutilangiza. 
2 Kunena kwakuti thambo ndi nthaka zidalengedwa m'masiku asanu ndi 
limodzi, amene akudziwa za masiku asanu ndi limodziwo momwe adalili ndi 
Mulungu yekha. Ndiponso mpandowo sitikudziwa tsatanetsatane 
wake.Chimene chilipo kwa ife nkukhulupirira basi. 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



457 



M *>i 



S \ SjJb 5j^-» 



m'nthawi yodziwika (ndi 
kukhazikitsidwa ndi Ife), akunena 
(mwamwano): "Nchiyani 
chikumanga chilangocho (kuti 
Chidze)? "Tamverani! Tsiku 
lomwe Chidzawadzera, 
sichidzachotsedwa kwa iwo Ndipo 
zomwe adali kuzichita 
mwachibwana Zidzawazinga. 

9. Ndipo munthu tikamulawitsa 
mtendere Wochokera kwa Ife, 
kenako nkuuchotsa Kwa iye, 
ndithu, amakhala wotaya mtima 
Kwambiri ndikukhala 
wosathokoza. 

10. Koma ngati titamulawitsa 
mtendere Pambuyo pa masautso 
omwe adamkhudza, Amati: 
"Masautso andichoka,"(ndipo 
Sakhala wotanganidwa ndi ntchito 
Zabwino zosonyeza kuyamika 
Mulungu), Choncho (tsopano) 
amakhala wosangalala 

11. Koma amene apirira ndi 
Kumachita ntchito zabwino, 
iwowo Ndiwo adzapeza 
chikhululuko Ndi malipiro aakulu 
(kwa Mulungu). 

12. Mwina usiya zina mwa 
zomwe Zikuvumbulutsidwa kwa 
iwe ndikubanika Nazo mchifuwa 
mwako chifukwa Chakuti 
akunena: "Bwanji sizidatsitsidwe 
Kwa iye nkhokwe zachuma kapena 



^ 


















Sural 11. Hud 



Juzu 12 



458 



U *;*■» 



^ ^ ^ a^j-* 



bwanji Mngelo osadza pamodzi 
ndi iye?" Koma ndithu, iwe ndiwe 
mchenjezi Basi ndipo Mulungu 
ndiye Muyang'aniri Wachinthu 
chilichonse. { 

13. Kapena akunena kuti: 
"Waipeka Qur'an?" Nena: 
"Tabweretsani Sura Khumi 
zopekedwa zomwe Zingafanane 
ndi iyi (Qur'an) ndipo aitaneni 
amene Mungathe (kuwaitana) 
kupatula Mulungu. (Adze 
akuthandizeni kulemba Bukulo) 
Ngati mukunena zoona!" 

14. "Ngati sakuyankhani, 
choncho, dziwani Kuti 
lavumbulutsidwa M'kudziwa kwa 
Mulungu, Ndikuti kulibe Mulungu 
wina koma Iye. Nanga kodi inu 
simugonjera Iye?" 

15. Amene akufuna moyo 
wadziko lapansi Ndi zokometsera 
zake, tiwapatsa pompo Padziko 
lapansi (malipiro a) zochita Zawo 
mokwanira, ndipo iwo m'menemo 
Sachepetseredwa chilichonse. 

16. Iwo ndi omwe sadzakhala 
ndi kanthu tsiku La chimaliziro 
koma moto basi. Ndipo Zimene 









Ophatikiza Mulungu ndi zina zake adali kupereka maganjzo kwa Mtumiki 
akuti ampemphe Mulungu kuti adzetse milumilu yachuma kapena 
amutumizire angelo kuti aziyenda naye limodzi. Ndipo adalinso kumaichitira 
Qur'an chibwana Mtumiki akawawerengera. Potero Mtumiki (SAW) adali 
kubanika mumtima mwake akafuna kufikitsa uthenga kwa iwo chifukwa 
chakuopa kutsutsidwa ndi kumchitira chibwana. 



Su rat 11. Hud 



Juzu 12 



459 



U *>» 



> ^ ^ 5jj- 



adachita m'menemo 
zidzaonongeka, Ndiponso 
nzopanda phindu Zimene 
ankachita. 

17. Nanga kodi munthu yemwe 
ali ndi chisonyezo Choonekera 
chochokera kwa Mbuye wake 
(Kotero kuti m'moyo mwake 
akuyenda molungama; Yemwe ndi 
mneneri Muhammad {SAW}) 
Ndipo Mboni ili naye pamodzi 
ikumtsata yochokera Kwa lye 
(Mbuye wake yomwe ndi Qur'an 
kapena Gaburiel) ndipo patsogolo 
pake padali Buku la Musa lomwe 
lidali chitsanzo Chabwino ndi 
mtendere, (wotereyu angafanane 
Ndi yemwe ali mum'dima wa 
umbuli yemwenso Sadziwa 
cholinga chakulengedwa kwake?) 
Awa ndi amene (aongoka) 
akulikhulupirira (Buku ili la 
Qur'an) ndipo amene ati 
Asalikhulupirire m'magulu (a 
adani), Moto ndiwo malo awo 
alonjezo. Choncho, Usakhale ndi 
chipeneko pa ichi; ndithudi Ichi 
ndi choona chochokera kwa 
Mbuye Wako koma anthu ambiri 
sakhulupirira. 

18. Ndipo palibe oipa kwambiri 
kuposa Yemwe wapeka bodza 
pakunamizira Mulungu (kuti ali 
ndi mwana ndi Athandizi). Iwo 
adzawabweretsa Kwa Mbuye 



«$*§&«$&& 






®, 



' 9* VSi 



vy&& 






Suratll.Hud 



Juzu 12 



460 I 1 1 *>» 



^ ^ syi Sjj^» 



wawo (tsiku la Kiyama) Ndipo 
mboni (zomwe ndi angelo) 
Zidzanena; "Awa ndi omwe 
Adapekera Mbuye wawo bodza. 
Mverani! Temberero la Mulungu 
Lili pa ochita zoipa kwambiri. 

19. Omwe akuletsa anthu 
kutsata Njira ya Mulungu ndi 
kufuna Kuikhotetsa (njirayo). 
Ndiponso iwo sakhulupirira za 
Tsiku lomaliza." 

20. Iwowa sangathe 
kumulepheretsa Mulungu 
M'dziko, ndiponso alibe atetezi 
Pambuyo pa Mulungu. Chilango 
chawo chidzaonjezeredwa 
(Chifukwa cha zoipa zawo). Sadali 
Kutha kumva ngakhale kuona 
(Chifukwa cha mkwiyo umene 
udali M'mitima mwawo wokwiira 
choonadi). 

21. Awa ndi omwe adziononga 
okha Ndipo zomwe adali kuzipeka 
Zidzawataika. 

22. Zoonadi, iwo ndi otaika 
Kwakukulu pa tsiku lomaliza. 

23. Ndithu, amene akhulupirira 
ndi Kumachita zabwino ndi 
kumadzichepetsa Kwa Mbuye 
wawo, iwowo Ndiwo anthu a ku 
Munda wa Mtendere. M'menemo 
adzakhala Muyaya. 

24. Fanizo la magulu awiriwa 
(Asilamu Ndi osakhulupirira), lili 



"^^IcPAW^ 



S 9 9 . V 9 ? 






©, 



G&$\>%8\&J&& 






s&j&e-^ 



iSS^SSJ^S^lfi 



Surat 11. Hud 



Juzu 12 



461 



It *>» 



\ \ ijA jj~* 



ngati (Munthu) wakhungu ndi 
gonthi, ndi (Munthu) wopenya ndi 
wakumva. Kodi awiriwa angakhale 
ofanana (Pa chikhalidwe chawo)? 
Bwanji simukuganiza? 1 

25. Ndipo ndithu, Ife tidamtuma 
Nuhi (Monga Mtumiki) kwa anthu 
ake (Kuti akawauze): "Ine kwa inu 
Ndine mchenjezi wofotokoza 
(Chilichonse); 

26. Ndikuti musapembedze 
aliyense Koma Mulungu basi. 
Ndithu, Ine ndikukuoperani 
chilango cha Tsiku lalikulu 
lopweteka (ngati Inu mupembedza 
milungu yabodza".) 

27. Ndipo pompo akuluakulu 
mwa omwe Sadakhulupirire mwa 
anthu ake, Adati: "Sitikukuona 
koma ndiwe Munthu monga ife, 
ndipo sitikukuona koma kuti 
akutsata anthu a pansi pathu 
ofooka panzeru (Omwe 
sadalingalire mozama za iwe). 
Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi 
Ulemerero ndi ubwino wochuluka 
Kuposa ife. Koma 
tikukuganizirani Motsimikiza kuti 
ndinu onama." 

28. (lye) adati: "E inu anthu 
anga! Kodi muona bwanji ngati 
ndili ndi Chisonyezo chowonekera 















**"" 






1 Imam Zamahashariyi adati: "Adawafanizira osakhulupirira ngati akhungu ndi 
agonthi, ndipo okhulupirira ngati openya ndi akumva". 



Su rati 1. Hud 



Juzu 12 



462 



\y *>i 



\ ^ sy* qjj~> 



chochokera kwa Mbuye Wanga 
ndipo wandipatsa chifundo 
chochokera Kwa lye (monga 
uneneri), ndipo Nkukhala 
chosokonezeka kwa inu, Kodi 
tingakukakamizeni kuvomereza 
Pomwe simukufuna?" 

29. "Ndipo E inu anthu anga! 
Ine sindikukupemphani Chuma pa 
uthengawu. Palibe Malipiro a ine, 
koma ali kwa Mulungu Basi. 
Ndipo ine sindingathamangitse 
Amene akhulupirira (monga 
Momwe mudandipemphera kuti 
Ndiwathamangitse anthu ofooka 
kuti Inu mulowe m'malo mwawo), 
ndithu Iwo adzakumana ndi 
Mbuye wawo, ndipo ine 
Ndikukuonani monga anthu 
osazindikira (mbuli). 

30. "Ndipo E inu anthu anga! 
Ndani Angandithandize kwa 
Mulungu ngati 
Nditawathamangitsa? Kodi 
simuganiza? 

31. "Ndipo ine sindikukuuzani 
kuti Ndili ndi nkhokwe zachuma 
cha Mulungu kapena kuti ine 
Ndikudziwa zinthu zamseri, 
ndiponso Sindinena kuti ndine 
m'ngelo. Ndiponso sindinena kwa 
omwe Maso anu akuwachepetsa 
kuti Mulungu sadzawapatsa 
chabwino. Mulungu akudziwa 
zam'mitima Mwawo. (Ngati 















SO rat 11. Hud 



Juzu 12 



463 * t *jA-i 



^ ^ ^^a ^jj* - 



nditatero) Ndiye kuti ine 
pamenepo Ndili m'gulu la oipa." 

32. (Iwo) adati: "E iwe Nuhi! 
Watsutsana Nafe, ndipo 
wachulukitsa kutsutsana Nafe. 
Choncho bweretsa kwa ife 
Chimene ukutilonjezacho, ngati 
ulidi Mmodzi mwa onena zoona. 

33. Adati: "Ndithu, Mulungu 
Achibweretsa kwa Inu ngati afuna, 
ndipo Inu simungathe 
Kumulepheretsa (chimene 
wafuna). 

34. "Ndipo kulangiza kwanga 
Sikungakuthandizeni ngati Ntafuna 
kukulangizani ngati Mulungu 
akufuna kukulekelerani Kusokera. 
lye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa 
lye mudzabwezedwa." 

35. Kapena akunena 
(osakhulupirira Am'Makka kuti: 
"Muhammad) Waipeka (Qur'an 
mwa iye yekha)"? Nena ngati 
ndayipeka ndiye Kuti machimo 
ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo 
ine ndili kutali Ndi chiweruzo 
chanu cha zoipa Zimene 
mukuchita. 

36. Ndipo tidamuululira Nuhi 
kuti: "(Tsopano) sakhulupirira 
aliyense Mwa anthu ako kupatula 
okhawo Akhulupirira kale. 
Choncho, Usadandaule pazimene 
Adali kuchita. 


















Suratll.Hud 



Juzu 12 



464 



IT tj±\ 



S \ ^jA 5jj-u 



37. Ndipo khoma chombo 
moyang'aniridwa Ndi Ife, ndi 
ulangizi wathu (satha Kukuchitira 
choipa), ndipo usandiyankhulitse 
Za iwo amene achita Zoipa (kuti 
ndiwakhululukire). Ndithudi, Iwo 
amizidwa." 

38. Ndipo adayamba kukhoma 
chombo. Nthawi iliyonse 
akamdutsa akuluakulu a Mwa 
anthu ake, adali kumchitira 
chipongwe. Naye ankanena (kuti): 
"Ngati inu Mukutichitira 
chipongwe, nafenso 
Tidzakuchitirani chipongwe 
monga Momwe mukutichitira 
chipongwe." 

39. "Posachedwa mudziwa kuti 
ndani Chimdzere chilango 
chomuyalutsa Ndikumtsikira 
chilango chopitirira." 

40. Kufikira pamene lidadza 
lamulo lathu, madzi Naphulika 
muuvuni, (chomwe chidali 
Chisonyezo chaNuhi chosonyeza 
Kudza kwa lamulo loona kwa 
anthu ake) Tidamuuza (kuti): 
"Kweza m'menemo (M'chombo) 
mtundu uliwonse (wa Nyama), 
ziwiriziwiri, (yaikazi Ndi 
yaimuna), ndi anthu a Kubanja 
lako kupatula omwe Chiweruzo 
(cha Mulungu) chatsimikizidwa pa 
iwo (kuti aonongeke), Ndipo 
(atengenso onse) amene 









tia/*-*' 



&&P 









Suratll. Hud 



Juzu 12 



465 



It *>■! 



^ ^ ay* 3jj-» 



Akhulupirira." Komatu ndi ochepa 
Kwambiri amene adakhulupirira 
Pamodzi ndi iye. 

41. Ndipo (Nuhi) adati: 
"Kwerani M'menemo mwadzina la 
Mulungu Mkuyenda kwake ndi 
mkuima kwake. Ndithu Mbuye 
wanga Ngokhululuka Kwambiri, 
Ngwachisoni." 

42. Ndipo chombocho chidali 
chikuyenda Nawo m'mafunde 
onga mapiri, ndipo Nuhi adaitana 
mwana wake yemwe adali Patali 
(atakana kulowa m'chombo): 
"Mwana wanga! Kwera pamodzi 
ndi ife Usakhale pamodzi ndi 
Osakhulupirira." 

43. (Iye) adati: "Ndithawira 
kuphiri Likanditeteza kumadziwa." 
Nuhi adati: "Lero palibe 
otetezedwa ku Lamulo la Mulungu 
kupatula Yemwe Mulungu 
Wamchitira chifundo." Pompo 
mafunde adatchinga pakati pawo. 
Choncho adali mgulu la omizidwa. 

44. Ndipo (pambuyo 
poonongeka onse ndi Zonse 
zomwe Mulungu adafuna kuti 
Zionongeke), kudanenedwa: "E 
iwe nthaka! Meza madzi ako, 
"Ndipo iwe Thambo! Amange 
(madzi ako amvula)." Choncho, 
madzi adaphwa ndipo lamulo 
Lidakwaniritsidwa. (Loononga 



vyi^i^sgsat 



•• 



® 



<»» <9*l'.\'? ' ,4\\' >*>' 



1&BU 



'JU 












®&^» 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



466 



It pjk-\ 



\ \ i^ft 5jj- 



anthu Oipa). Ndipo (chombo) 
chidaima Pamwamba pa (phiri 
lotchedwa) Judi, Ndipo 
kudanenedwa: "Aonongeke Onse 
ochita zoipa." 

45. Ndipo Nuhi adafuulira 
Mbuye wake Nati. "E Mbuye 
wanga! Ndithu, Mwana wanga ali 
mgulu la akubanja langa 
(Akuonongedwa). Ndipo ndithu, 
Lonjezo lanu ndiloona, ndipo Inu 
Ndinu Woweruza mwachoonadi 
kuposa Aweruzi onse." 

46. (Mulungu) adati: "E iwe 
Nuhi! Ndithu, iyeyo simwana wa 
m'banja Lako. lye zochita zake 
Sizili zabwino. Choncho 
Usandipemphe zomwe 
siukuzidziwa Ine ndikukulangiza 
(kuti) usakhale M'gulu la 
osazindikira (mbuli)." 

47. (Nuhi) adati: "E, Mbuye 
wanga! Ndikudziteteza mwa Inu 
kuti Ndisakupempheninso zomwe 
sindikuzidziwa. Ngati 
simundikhululukira Ndi 
kundichitira chifundo, Ndikhala 
mwa anthu otaika." 

48. Kudanenedwa: "E, iwe 
Nuhi! Tsika (Pa nthaka youma) 
mwamtendere Wochokera kwa Ife, 
ndipo madalitso Ambiri akhale pa 
iwe ndi Pa anthu omwe ali nawe; 
ndipo Kudzakhala mibadwo ina 















Su rat 11. Hud 



Juzu 12 



467 



\y *>-i 



> > SjJb Sjj-** 



(yoipa Pambuyo pako) yomwe 
tidzaisangalatsa, Ndipo kenako 
chidzaikhudza Chilango chowawa 
chochokera Kwa Ife." 

49. Izi ndi zina mwa nkhani 
zobisika zomwe Tikukuululira iwe. 
Siudali kuzidziwa, Iwe ngakhale 
anthu ako, patsogolo Pa ichi, 
(Qur'an isadadze). Choncho, 
pirira. Ndithu, mathero Abwino 
adzakhala kwa anthu oopa 
Mulungu. 

50. Ndipo anthu amtundu wa 
Adi, tidawatumizira mbale wawo 
Hud. Adati: "E inu anthu anga! 
Pembedzani Mulungu! (Siyani 
kupembedza Mafano). Mulibe 
Mulungu wina Koma lye. Inu 
simuli kanthu Koma ndinu opeka 
bodza (n'kunena Kwanu kwakuti 
mafano ndi anzake A Mulungu) 

51. "E inu anthu anga! 
Sindikukupemphani Malipiro pa 
ichi (uthengawu). Palibe Malipiro 
anga koma ali kwaYemwe 
Adandilenga. Kodi mulibe nzeru? 

52. Ndipo E inu anthu anga! 
Pemphani Chikhululuko kwa 
Mbuye wanu, (Pamachimo omwe 
mwakhala mukuchita), Kenako 
lapani kwa lye. Akutumizirani 
Mitambo yodzetsa mvula yambiri, 
Ndipo akuonjezerani mphamvu pa 
Mphamvu zanu (zomwe muli 






rrfii i 



IUA 









Suratll.Hud 



Juzu 12 



468 



>y fr>i 



> \ syt ojj^ 



nazo). Choncho, musatembenuke 
kukhala oipa" 

53. (Iwo) adati: "E iwe Hud! 
Sudatibweretsere Chisonyezo 
chooneka (chosonyeza Kuti ndiwe 
Mneneri), ndipo ife sitisiya 
(Kupembedza) milungu yathu 
chifukwa cha Zoyankhula zakozo. 
Ndipo ife sitikukhulupirira" 

54. "Sitinena kanthu, koma kuti 
(mwina) Milungu yathu ina 
yakulodza Misala." (lye) adati: 
"Ndithu, ine Ndikupereka umboni 
kwa Mulungu ndipo inunso 
Perekani umboni kuti ine ndili 
Kutali ndi zimene mukumphatikiza 
nazo (Mulungu pomazipembedza), 

55. Kusiya lye; (milungu 
yanuyo sindikuiopa Ngati ili ndi 
mphamvu pamodzi ndi inu) 
Ndichitireni chiwembu Nonsenu, 
ndipo kenako 
musandiyembekezere 
(Musandipatse nthawi). 

56. Ndithu, ine ndatsamira kwa 
Mulungu, Mbuye wanga ndiponso 
Mbuye wanu. Palibe Cholengedwa 
chilichonse koma Mulungu 
Wachigwira tsumba lake 
(ndikuchiyendetsa Mmene 
akufunira). Ndithudi, Mbuye 
Wanga Ngwachilungamo. 

57. Ngati munyoza (kulandira 
chimene Ndakuuzani palibe vuto 



'^5}%S&£&k* 



'Zti'A.i 












*'l.'i'A. 



^m^<m^^ 






% 



>£*> 



)&i&Xl®f&$® 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



469 



>r *j*-i 



> ^ i^ft Ojj-- 



kwa ine); Ndithu, ndafikitsa kwa 
inu Chimene ndatumidwa. Ndipo 
Mbuye wanga (awaononga 
Osakhulupirira) ndi kubweretsa 
Anthu ena m'malo mwanu, ndipo 
Inu simungamusautse konse. 
Ndithu, Mbuye wanga ndi Msungi 
Wa chilichonse. 

58. Ndipo pamene lamulo lathu 
lidafika (Lakuwaononga), 
tidampulumutsa Hud ndi amene 
adakhulupirira Pamodzi naye, 
mwachifundo Chathu, Ndipo 
tidawapulumutsa kuchilango 
Chokhwima. 1 

59. Ndipo awa ndi Adi. 
Adatsutsa Aya za Mbuye wawo 
ndi kunyoza Atumiki Ake; ndipo 
adatsata Lamulo la yense 
wodzikweza, Wamakani. 

60. Ndipo adawapachika 
matemberero Pa moyo wapano 
padziko lapansi Ndi tsiku la 
Kiyama (tsiku la Chiweruzo). 
Dziwani! Ndithu, Adi adakana 
Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka 
Adi, anthu a Hud!. 

61. Ndipo kwa anthu amtundu 
wa Samud, (Tidatuma) m'bale 
wawo Swaleh. Adati: "E inu anthu 


















1 Chilangocho chidali chimphepo choononga chomwe chinagumula nyumba 
ndi kulowa m'mphuno za adani a Mulungu ndi kutulukira kokhalira kwawo. 
Chinkangowagwetsa chafufumimba kotero kuti anthu adali lambilambi ngati 
mathunthu a mitengo ya kanjedza. 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



470 



\y *>l 



> ) sy* djf* 



anga! Lambirani Mulungu. Mulibe 
Mulungu wina koma lye yekha. 
lye Adakuumbani ndi nthaka ndi 
kukukhazikani M'menemo.Ndipo 
mpempheni Chikhululuko (pa 
zolakwa zanu), Kenako 
tembenukirani kwa lye. Ndithu, 
Mbuye wanga ali pafupi (Ndi 
akapolo Ake). Ndipo Ngovomera 
mapempho (aopempha)". 

62. Iwo adati: "E iwe Swaleh! 
Ndithudi, udali woyembekezeka 
(Kukhala mfumu kwa ife) 
patsogolo Pa izi (usanabwere ndi 
izi). Ha! Kodi ukutiletsa 
kuwalambira omwe makolo Athu 
adali kulambira? Ndithu, ife Tili 
m'chikaiko chokaikira zomwe 
Ukutiitanirazo." 

63. (lye) adati: "E inu anthu 
anga! Mukuona bwanji ngati ndili 
ndi Chisonyezo choonekera 
chochokera kwa Mbuye wanga 
(chosonyeza kuona kwa 
Zimenezi), nandipatsanso chifundo 
Chochokera kwa lye. Nanga ndi 
Yani angandipulumutse 
kuchilango Cha Mulungu ngati 
nditamunyoza? Choncho, 
simungandionjezere China chake 
koma kutaika basi. 

64. "Ndipo E inu anthu anga! 
Iyi ngamira Ya Mulungu ndi 
chisonyezo kwa Inu. Ilekeni izidya 
panthaka Ya Mulungu, ndipo 









9 \ 6 'V* 9,<9}9 '\''^JJ " *l 1 l 






Siiratll.Hud 



Juzu 12 471 \ r tjA-i 



S \ ijjfc djj^i 



musaikhudze Ndi choipa kuopa 
kuti chilango Chachangu 
chingakuonongeni . " ' 

65. Koma adaipha. Choncho 
(Swaleh) Adati: "Sangalalani 
m'midzi Yanuyi pamasiku atatu. 
(kenako Mulangidwa). Limenelo 
ndi lonjezo Osati labodza." 

66. Choncho pamene lamulo 
Lathu Lidadza (lakuononga 
midziyo), Tidampulumutsa Swaleh 
ndi anthu Amene adakhulupirira 
naye, Kukuyaluka kwa tsiku 
limenelo, Mwa chifundo chathu. 
Ndithu, Mbuye wako ndi Mwini 
mphamvu, Ngopambana. 

67. Ndipo amene adadzichitira 
okha Zoipa phokoso lalikulu 
lidawaononga, Tero kudawachera 
m'nyumba Zawo ali lambilambi 
(atafa) 

68. Ngati kuti iwo mudalibemo 
m'menemo. Mverani! Ndithu, 
Asamudu adamkana Mbuye wawo. 
Choncho Asamudu Adaonongeka. 

69. Ndipo ndithu, atumiki athu 
(angelo) Adadza kwa Ibrahim ndi 
uthenga Wabwino. (Iwo) adati: 






^&$£$£Z'$&Jfc 



^j&jt»ti&M> 






&P&&tojffij$$& 



i) • » u* *h X' 9 \ 






1 Asamudu adampempha chozizwitsa Mneneri wawo Swaleh chotsimikiza kuti 
iye adalidi Mneneri wa Mulungu. Chozizwitsa chomwe adampempha nkuti 
atulutse ngamira patanthwe. Choncho mwamphamvu za Mulungu ngamira 
idatuluka m'tanthwemo. Ndipo adawauza kuti asaichitire choipa. Aisiye 
izingodzidyera m'dziko la Mulungu. Koma iwo adaipha, ndipo chilango cha 
Mulungu chidawatsikira. 



Su rat 11. Hud 



Juzu 12 472 > Y %^r\ 



\ \ SjJb Qjj** 



"Mtendere!" (lye) adayankha 
"Mtendere (ukhale pa inu!)" Ndipo 
(Ibrahim) sadakhalitse 
(Adafulumira) kudza nayo nyama 
Yootcha ya thole (mwana wa 
ng'ombe) 

70. Koma pamene adaona kuti 
manja Awo sakuwatambasula 
kuchakudya Adawadodoma, 
Nadzadzidwa nawo mantha. (Iwo) 
Adati: "Usaope; ndithu, ife 
Tatumidwa kwa anthu a Luti (kuti 
Tikawaononge ndiponso kukupatsa 
Nkhani yabwino)." 

71. Ndipo (m'menemo nkuti) 
Mkazi wake (wa Ibrahim) Ali 
chiimire, ndipo adaseka. Kenaka 
tidamuuza uthenga wabwino 
(Wakubadwa kwa) Isihaka ndipo 
Pambuyo pa Isihaka, Yakubu . 

72. (lye) adati: "Kalanga ine! 
Ndibereka pomwe ine ndili 
Nkhalamba, ndiponso uyu 
Mwamuna wanga ndi nkhalamba? 
Ndithudi, ichi ndi chinthu 
Chododometsa." 

73. (Angelowo) adati: 
"ukudabwa Ndi lamulo la 
Mulungu? Chisomo Cha Mulungu 
ndi madalitso Ake Zili pa inu, E 
inu eni nyumba iyi! lye 
Ngoyamikidwa, Mwini ulemelero!" 

74. Ndipo pamene Ibrahim 
mantha adamchokera 



«$W»fc3 












4^M?&s&s®$ 



^^m^&w®* 



& 



'*te}&y*&<tix$i 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



473 



>T t,jfr\ 



> ^ i^A *jj~* 



Ndikumufikira uthenga wabwino, 
Adayamba kutidandaulira za anthu 
a Luti (kuti tisawaononge). 

75. Ndithu, Ibrahim adali 
wodekha Wodandaulira Mulungu, 
wobwerera Kwa lye mwachangu, 

76. (Tidamuuza): "E, iwe 
Ibrahim! Siya ichi. Lamulo la 
Mbuye wako, Ndithu, ladza. Ndipo 
ndithu, iwo Chiwadzera chilango 
chosabwezedwa. 

77. Ndipo atumiki athu pamene 
adafika Kwa Luti, iye anadandaula 
za iwo Ndi kubanika mumtima 
(chifukwa Chosowa njira 
yowatetezera kwa Anthu oipa 
pomwe iye sadadziwe Kuti 
alendowo ndi Angelo), Nati: "Lino 
ndi tsiku lovuta". 

78. Ndipo anthu ake adadza 
akuthamangira Kwa iye (ku 
nyumba kwake Kuti adzachite 
zauve ndi alendowo). Ndipo 
kalenso ankachita zoipa 
zokhazokhazi (Luti) adati: "E 
anthu Anga! Nawa asungwana 
anga; Ngoyenera kwa inu 
(kuwakwatira, Osati amuna 
anzanu) choncho, Opani Mulungu, 
ndipo musandiyalutse Pamaso pa 
alendo anga. Kodi mwa inu Mulibe 
munthu woongoka?" 

79. (Iwo) adati: "Ndithu, 
ukudziwa Bwino kuti tilibe 












^dSu&^uS&jitf 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



474 



^r *jk* 



\ \ *y* 5 jj~- 



khumbo ndi Atsikana ako. Ndipo 
ndithu, iwe Ukudziwa bwino 
chimene tifuna". 

80. (lye) adati: "Ndikadakhala 
nayo Mphamvu (yomenyana nanu) 
kapena Kotsamira kolimba 
kwamphamvu (Ndikadalimbana 
nanu kuti musachite Zauve ndi 
alendowa)". 

81. (Athengawa) adati: "E iwe 
Luti! Ife Ndi athenga a Mbuye 
wako. Safika kwa Iwe (ndi 
chilichonse choipa). Ndipo Choka 
pamodzi ndi banja lako m'gawo la 
Usiku, ndipo aliyense wa inu 
asatembenuke (Kuyang'ana 
m'mbuyo akamva mkokomo 
Wakudza kwa chilangocho), 
kupatula Mkazi wako; iye 
chimpeza chimene chiwapeze 
Anthu enawo. Ndithu, lonjezo 
lawo ndi M'mawa. Kodi m'mawa 
suudayandikire?" 

82. Choncho, pamene lidadza 
lamulo lathu, Tidaugadabula 
(m'zindawo) kumwamba Kukhala 
pansi, pansi kukhala kumwamba, 
Ndipo tidawavumbwitsira mvula 
ya Sangalawe zopangika ndi dongo 
lotentheka Ndi moto, zogwirana 
kwambiri. 

83. (Sangalawezo) zokhala ndi 
zizindikiro Kwa Mbuye wako. 
(sangalawe iliyonse Idali ndi 






<s^%^*^ (jrsifcM 



V 9 K 9 W \ 9 * 



s ' . (V •* *'*«"' * 9 £, ' * 






©"rt^j^l 



Sural 11. Hud 



Juzu 12 



475 



>Y *>t 



^ ^ ^yb 5jj-> 



mwini wake); ndipo chilango 
Chimenechi sichili kutali ndi anthu 
Oipa. 

84. Ndipo,ku Madiyani 
tidamtuma m'bale wawo Shuaibu 
iye adati: "E inu anthu anga! 
Pembedzani Mulungu; mulibe 
Mulungu wina koma Iye. Ndipo 
musachepetse mulingo wa mbale 
Ndi wasikelo (powapimira anthu) 
Ine ndikukuonani kuti ndinu Opeza 
bwino, ndipo ndikukuoperani 
Chilango cha tsiku lalikulu Lomwe 
lidzakuzingani. 

85. Ndipo E inu anthu 
anga!Kwaniritsani Mulingo 
wambale ndi wasikero 
Mwachilungamo, ndipo 
musawachepetsere Anthu zinthu 
zawo (mwachinyengo). Ndipo 
musafalitse zoipa padziko ndi 
Cholinga chodzetsa chisokonezo. 

86. Chuma chimene wakusiirani 
Mulungu (m'njira yovomerezeka) 
Ndicho chabwino kwa inu ngati 
Muli okhulupirira. Ndipo ine 
Sindine msungi wanu". 

87. Adati: "E iwe Shuaib! Kodi 
Mapemphero ako akukulamula 
(Kuti utilamule) kuti tisiye Zimene 
makolo athu ankapembedza, 
kapena kuti tisiye Kuchita zimene 
tifuna pachuma Chathu? Ndithudi, 
iwe ndiwe Wanzeru, ndi 















G^j"^ 



Suratll.Hud 



Juzu 12 476 > Y *j*-i 



> > ijA Ojj-* 



wolungama." (Izi Adali kumnenera 
m wachipong we) . 

88. (lye) adati: "E inu anthu 
anga! Mukuona bwanji ngati ndili 
ndi Chisonyezo chochokera kwa 
Mbuye Wanga, ndipo nkundipatsa 
riziki Labwino (lahalali) lochokera 
Kwa lye, (ndisiye zimenezi ndi 
Kusankha njira yokhota)? Ndipo 
sindifuna kusiyana nanu Pochita 
chimene ndakuletsani. Sindifuna 
china, koma kukonza Mmene 
ndingathere; ndipo Kupambana 
kwanga (pazimenezi) Kuli kwa 
Mulungu. Kwa lye Ndatsamira, 
ndipo kwa lye Ndikutembenukira. 

89. "Ndipo E inu anthu anga! 
Kutsutsana Nane 
kusakuchimwitseni kuopera Kuti 
chingakupezeni chonga chimene 
Chidawapeza anthu a Nuhi kapena 
Anthu a Hud kapenanso anthu a 
Swaleh; ndipo anthu a Luti sali 
Kutali ndi inu. 

90. "Ndipo mpempheni 
chikhululuko Mbuye wanu ndipo 
lapani kwa lye (Posiya machimo 
ndikuchita zabwino). Ndithu, 
Mbuye wanga Ngwachisoni 
Ngwachikondi chochuluka (Kwa 
anthu ake)." 

91. (Iwo) adati: "E, iwe 
Shuaib! Sitikumvetsa zambiri 
mwazomwe Ukunena. Ndipo ife 


















Suratll.Hud 



Juzu 12 477 I ) t tjJt-i 



> > SjA jj~- 



tikukuona Wofooka mwa ife. 
Pakadapanda Akubanja lako, 
tikadakugenda ndi Miyala. Ndipo 
ulibe ulemerero Pa ife (koma 
tikusunga ulemu wa Anthu 
akubanja lako)." 1 

92. (lye) adati: "E inu anthu 
anga! Kodi anthu akubanja kwanga 
ndiwo Olemekezeka kwambiri 
kwa inu Kuposa Mulungu? Ndipo 
mwamuyika lye (Mulungu) 
kukhala kumbuyo Kwa misana 
yanu. Ndithu, Mbuye Wanga zonse 
zimene mukuchita Akuzidziwa 
bwinobwino. 

93. "Ndipo E anthu anga! 
Chitani (zimene Mufuna) mmene 
mungathere; inenso Ndichita 
chimodzimodzi (mmene 
Ndingathere). Posachedwapa 
mudziwa ndani Chimufike 
chilango chomsambula, ndipo 
Ndani wabodza. Ndipo dikirani 
inenso Ndidikira pamodzi ndi inu." 

94. Ndipo pamene lamulo lathu 
lidadza, Tidampulumutsa Shuaib 
pamodzi ndi amene 
Adakhulupirira naye, 
mwachifundo Chathu. Ndipo 
amene adachita Zoipa, phokoso 
lidawachotsa moyo, Tero 



®^^M^^^^^i 









& 

& 

l >*.*"'<"' 






1 Anthu ake ankamuuza izi zoti sakumvetsa zomwe iye anawauza 
mwachibwana, nawafanizira malangizo akewo monga malangizo a munthu 
wozunguzika nzeru. 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



478 



^r *>i 



\ \ Sj* Ojj-4 



kudawachera M'nyumba zawo ali 
lambilambi (atafa) 

95. Ndiye ngati sadakhalemo, 
tamverani! Adaonongeka (anthu) a 
ku Madiyani Monga momwe 
adaonongekera a Samudu! 

96. Ndipo ndithu, tidamtuma 
Musa pamodzi ndi Zozizwitsa 
zathu ndi maumboni Oonekera. 

97. Kwa Farawo ndi nduna 
zake. Koma iwo Adatsata lamulo 
la Farawo, ndipo Lamulo la 
Farawo siloongoka. 

98. Tsiku la Kiyama, (Farawo) 
Adzawatsogolera anthu ake ndi 
Kuwafikitsa ku moto. Ndipo 
taonani pamalo poipa kufikirapo. 

99. Iwo adatsatizidwa ndi 
temberero Pano padziko lapansi 
ndipo patsiku La Kiyama 
(adzatsatizidwanso) Taonani 
kuipa, mphoto (Yawo) yopatsidwa. 

100. Izi ndi zina mwa nkhani za 
m'mizinda (Zomwe) 
tikukusimbira.Ina Mwa iyo 
ikadalipobe, ndipo ina Idatha. 

101. Ndipo sitidawachitire 
choipa (Powaononga). Koma 
adadzichitira Okha zoipa 
(pakusakhulupirira Mulungu ndi 
kupembedza mafano Ndikuipitsa 
padziko); milungu Yawo yomwe 
ankaipembedza kusiya Mulungu, 















°*$ > -W 






Suratll.Hud 



Juzu 12 



479 



IT *>i 



\ ) SjA djj-- 



siidawathandize chilichonse 
Pamene lidadza lamulo la Mbuye 
wako (la kuwaononga). Ndipo 
(milunguyo) siidawaonjezere 
(China chake) koma chionongeko 
Basi. 

102. Ndipo mmenemo ndi 
momwe kumakhalira Kulanga kwa 
Mbuye wako pamene Alanga 
anthu a m'mizinda Akakhala oipa 
(pamakhalidwe). Ndithu, kulanga 
Kwake (Mulungu) Nkowawa, 
nkwaukali. 

103. Ndithu, m'zimenezi muli 
lingaliro Kwa yemwe akuopa 
chilango cha Tsiku lomaliza. 
Limenelo ndi Tsiku 
losonkhanitsidwa anthu. Ndipo 
limenelo ndi tsiku Lochitiridwa 
umboni (ndi Zolengedwa zonse). 

104. Ndipo sitikulichedwetsa 
koma m'nthawi Yowerengeka 
(kwa Mulungu, ngakhale Kuti kwa 
anthu likuoneka kuti lili Kutali.) 

105. Tsiku lakudza (zoopsa 
zake), Sazalankhula aliyense koma 
mwachilolezo Chake (Mulungu). 
Ena Adzakhala oipa, ndipo (ena) 
Adzakhala abwino. 

106. Tsono amene adzakhala 
oipa Kobwerera kwawo nkumoto. 
Iwo adzakhala m'menemo Akufuula 
potulutsa mawu ndi kuwabweza 
(Monga kulira kwa bulu). 









*&&$m®& 









Suratll.Hud 



Juzu 12 



480 1 1 >>i 



> > ayh ojj-u 



107. Adzakhala m'menemo 
kwa nthawi yonse Yomwe thambo 
ndi nthaka zidzakhalire, Kupatula 
Mbuye wako akadzafuna. Ndithu, 
Mbuye wako Ngochita chimene 
wafuna. 

108. Tsono amene adzakhale 
abwino adzakhala M'munda wa 
mtendere. Adzakhala mmenemo 
Kwa nthawi yonse yomwe thambo 
ndi Nthaka zidzakhalire, kupatula 
Mbuye wako Akadzafuna; zopatsa 
(za Mbuye wako Ndizo zopatsa) 
zosatha. 

109. Choncho, usakhale ndi 
chipeneko Pazimene awa 
akuzipembedza (Zakuti similungu 
yoona). Sapembedza koma 
momwe Amapembedzera makolo 
A wo kale. Ndipo ndithu, Ife 
Tiwapatsa gawo lawo (la chilango) 
Mokwanira popanda kuchepetsa. 

110. Ndipo ndithu, tidampatsa 
buku Musa, Koma kusiyana 
kudabuka mmenemo 
(Pakatanthauzidwe ka bukulo 
Pambuyo pa Musa). Pakadapanda 
Mawu a Mbuye wako omwe 
adatsogola (Oti sadzawalanga 
nthawi Isanafike),ndithu 
kukadaweruzidwa pakati pawo. 
Ndipo ndithu, iwo ali m'kukaika 
ndi kupeneka Kwakukulu 
pazimenezo. 















Suratll.Hud 



Juzu 12 



481 



U *j*-i 



> > ^ djj^ 



111. Ndipo ndithu, Mbuye wako 
Adzawapatsa onsewo mphoto 
Yazochita zawo mokwanira. Ndithu, 
lye Ngodziwa (zonse) Zimene 
akuchita. 

112. Choncho (E iwe Mtumiki!) 
Pitiriza kulungama monga momwe 
Akulamulira (iwe) pamodzi Ndi 
omwe atembenukira (kwa 
Mulungu), ndipo musapyole 
Malire. Ndithu, lye akuona Zonse 
zimene muchita. 

113. Ndipo musapendekere kwa 
amene Sali olungama kuopa kuti 
Chilango cha moto 
chingakukhudzeni; Ndipo 
simudzakhala ndi Atetezi kwa 
Mulungu, ndipo Potero 
simudzathandizidwa(Chilichonse). 

114. Ndipo pemphera Swala 
mbali ziwiri Za usana ndi nthawi 
za usiku Zomwe zili pafupi ndi 
usana. Ndithu, zabwino 
zimachotsa Zoipa. Ichi ndi 
chikumbutso Kwa okumbukira. 

115. Ndipo pirira (E! Iwe 
Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo 
a Mbuye Wako)! Ndithu, Mulungu 
sataya Malipiro a ochita zabwino. 



Iff < *iA'"b' <<i 






2* 



*2&& 






*Gs^%iS*mj& 



1 Apa akutanthauza kuti ngati chikhalidwe chamibadwo yakale chidali chonchi, 
mibadwo yomwe adaitumizira buku lake, natsutsana ndi bukuli, ena aiwo 
nalitaya kutaii, iweyo pitiriza ndi Asilamu omwe uli nawo kugwira njira 
yolungama monga momwe Mulungu wakulamulira. Usapyole malire 
ponyozera chimene chili choyenera iwe kuchichita, kapena kudzikakamiza 
chimene sungathe kuchichita. Mulungutu akudziwa zonse zomwe muchita 
ndipo adzakulipirani. 



Su rat 11. Hud 



Juzu 12 



482 



\y *jA-i 



\ \ SjA *J>^ 



116. Kodi bwanji sadakhalepo, 
Mumibadwo ya anthu akale, Eni 
nzeru (omvera Akalangizidwa), 
Oletsa kuononga padziko Kupatula 
ochepa amene Tidawapulumutsa 
Mwa iwo? Ndipo amene 
Adadzichitira okha zoipa adatsata 
Zomwe adasangalatsidwa nazo, 
Choncho, adali oipa. 

117. Ndipo Mbuye wako sali 
woononga Midzi mopanda 
Chilungamo pomwe Eni ake 
(midziyo) ali ochita zabwino. 

118. Ndipo Mbuye wako 
akadafuna, Anthu onse 
akadawachita kukhala Mumpingo 
umodzi. Choncho saleka Kukhala 
osiyana (maganizo), 1 

119. Kupatula omwe Mbuye 
wako Wawachitira chifundo; ndipo 
chifukwa Cha chifundocho, 
adawalenga (koma okha 
Akusankha zoipa). Ndipo mawu a 
Mbuye Wako akwaniritsidwa 
(akuti):"Ndithudi, Ndidzadzadzitsa 
Jahannama ndi ziwanda ndi 
Anthu onse pamodzi (omwe adali 
oipa)." 

120. Ndipo tikukusimbira zonse 
mwa Nkhani za aneneri zomwe 
tikukulimbikitsa nazo mtima. 















Akadawakakamiza onse kukhala mpingo umodzi. Koma adawapatsa nzeru 
ndi mphamvu yozindikirira zinthu kuti asankhe chomwe afuna, chabwino 
kapena choipa. 



Suratll.Hud 



Juzu 12 



483 



)1 *>i 



\ \ $j& &JJ~»» 



Ndipo M'zimenezi choonadi 
chakufika Ndi ulaliki ndiponso 
chikumbutso Kwa okhulupirira. 

121. Ndipo auze amene 
sadakhulupirire (Kuti); "Chitani 
Mmene mungathere; nafenso 
tichita (Mmene tingathere)". 

122. "Ndipo dikirani 
(chiweruzo cha Mulungu) nafenso 
tikudikira". 

123. Zonse zobisika 
zakumwamba ndi Pansi nza 
Mulungu ndipo zidzabwezedwa 
Kwa lye. Choncho, mpembedzeni 
ndi Kutsamira kwa lye. Ndithu, 
Mbuye wako siwonyalanyaza 
zimene Mukuchita. 










Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



484 



IT *>i 



^ T «-i—»jj *jj— » 




Sura ya Yusuf ndi imodzi mwa Sura zomwe 
zidavumbulutsidwa ku Makka ndipo ikunenetsa za nkhani ya 
mneneri wa Mulungu, Yusuf mwana wa Yakubu, ndi masautso 
osiyanasiyana amene adakumana nawo ochokera kwa abale ake 
omwe ankamchitira njiru. Ikufotokozanso za masautso omwe 
adakumana nawo m'nyumba ya Aziz wa ku Misir ndipo kenako 
nkukalowa m'ndende. 

Cholinga cha nkhaniyi ndikutonthoza mtima wa mtumiki 
Muhammad (SAW) kumasautso omwe amapezana nawo 
kuchokera kwa anthu ake. 




Surat 12. Yusuf Juzu 12 485 \ 1 *>i 



\ y UU>y *jj-j 



Surat Yusuf XII 



Life:*" 









^ ^^^^ai^ < <t--.^ u-ii 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Alif-Lam~Ra. Izi ndi aya za 
m'buku Lomwe likuonetsera 
poyera (chilichonse Chofunika). 

2. Ndithu, Ife taivumbulutsa 
Qur'an Ya Charabu kuti inu 
Muzindikire. 

3. Ife tikukusimbira nkhani 
zabwino Pokuzindikiritsa Qur'an 
iyi; ndithu, Udali mmodzi mwa 
osadziwa zinthu, Isanakufike. 

4. Akumbutse za Yusuf pamene 
adauza tate Wake: "E inu tate 
wanga! Ndithu, Ine ndaona kutulo 
nyenyezi khumi ndi Imodzi, dzuwa 
ndi mwezi, zonsezo Ndaziona 
zikundigwadira". 

5. (Tate wake) adati: "E iwe 
mwana wanga! Usawasimbire 
abale ako maloto ako Kuopa kuti 
angakuchitire chiwembu; Ndithu, 
Satana kwa munthu, ndi mdani 
Woonekera. ! 

6. Ndipo momwemo Mbuye 
wako Akusankha komanso 
akuphunzitsa Kumasulira 
nkhani(zamaloto) ndi 



qWllfc^JMt, 






© 












1 Sibwino munthu kufotokozera anthu chisomo chako chonse ngati palibe 
zofunikira kutero. Dziwani kuti mwini madalitso ngochitiridwa dumbo. 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



486 



>r frjA-i 



> T ei~»»jJ *JJ-" 



Kukwaniritsa mtendere Wake pa 
iwe, ndi Pambumba ya Yakubu 
monga momwe Adakwaniritsira 
kwa makolo ako kale, Ibrahim ndi 
Isihaka. Ndithu, Mbuye Wako 
Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya." 

7, Ndithu mwa Yusuf ndi 
abale Ake, muli malingaliro ambiri 
kwa ofunsa (Zinthu kuti adziwe). 

8, Kumbuka pamene (abale a 
Yusuf) adati: "Ndithu, Yusuf ndi 
m'bale wake (Benjamini) 
ngokondedwa kwa bambo Wathu 
kuposa ife pomwe ife ndife gulu 
Lamphamvu. Ndithu, bambo 
wathu ali Mkusokera koonekera 
(sadziwa yemwe Ali ndi 
chithandizo chokwanira)." 

9. Mupheni Yusuf kapena 
mukamponye kudziko (Lakutali), 
kuti nkhope ya Bambo wanu 
Ikutembenukireni (pakuti nthawi 
Imeneyo Yusuf sadzakhalapo, 
yemwe Akumkonda kwambiriyo); 
Ndipo pambuyo Pake (mutalapa 
tchimoli) mdzakhala Abwino, 
(kwa Mulungu)." 1 

10. Adanena wonena mwa iwo: 
"Musamuphe Yusuf, koma 
mponyeni m'chitsime chakuya; 









' 









1 Dyera loipa kwambin ndiko kunena koti: "Tandislyani ndichite machimo, 
kenako ndidzalapa." Dziwani kuti machimo omwe Mulungu angawakhululukire 
ngomwe munthu wawachita mosazindikira kapena kuti popanda kuwafunafuna, 
osati owachita mwadaladala ncholinga choti adzalapa pambuyo pake monga 
momwe abale ake a Yusuf ankaganizira. 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



487 I i y *>■> 



> Y <*J)-*tjt 6jj~* 



Adzamtola ena apaulendo ngati inu 
Mwalingadi kutelo." 

11. (Pambuyo pogwirizana 
paganizo lomuponya M'chitsime 
chakuya adapita kwa Bambo Wawo) 
anati: "E Bambo wathu! Kodi 
Bwanji simutikhulupirira pa Yusuf, 
Pomwe ife timamfunira zabwino? 

12. Mperekeni mawa pamodzi 
ndi ife (Kubusa) kuti akadye 
mokondwa ndi Kusewera; 
ndithudi, ife tikamsamala." 

13. (Bambo wawo) adati: 
"Ndithu, Zikundidandaulitsa 
Zakuti mupite naye; Ndikuopa kuti 
Angajiwe ndi mimbulu pomwe inu 
Simukulabadira za iye." 

14. (Iwo) adati: "Ngati mimbulu 
itamudya Pomwe ife ndife gulu 
lanyonga kwambiri, Ndiye kuti 
tidzakhala otaika. 

15. Ndipo pamene adanka naye 
ndi Kugwirizana pakati pawo kuti 
amuike Mchitsime chakuya, 
(adamuikadi) .Ndipo 
Tidamzindikiritsa iye (Yusuf): 
"Ndithu udzawauza chinthu 
chawochi (Chimene akuchitirachi) 
pomwe iwo sakudziwa." 

16. Ndipo adadza kwa Bambo 
wawo madzulo Akulira, 

17. Akunena: "E Bambo 
wathu! Tidapita Kokapikisana 









-~H$UPti?& 



^&p&ft$R$& 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



488 I > t *>■' 



) Y UJ~*»JJ *JJ—* 



(kuthamanga), ndipo Tidamsiya 
Yusuf pomwe padali ziwiya Zathu; 
choncho mimbulu yamudya Koma 
inu simutikhulupirira (pazimene 
Tikukuuzanizi) ngakhale kuti 
Tikunena zoona." 

18. Ndiponso adabwera ndi 
mkanjo wake (wa Yusuf )uli ndi 
magazi abodza. (Bambo wawo 
pamene Adauona mkanjo wo uli 
wosang'ambika) Adati: "Koma 
mitima yanu yakukometserani 
Chinthu (chomwe mwamchitira 
mnzanu Mwa chifuniro chanu; 
ndipo chimene ine Ndingachite 
ndi) kupirira kwabwino; ndipo 
Mulungu ndi Wopemphedwa 
chithandizo Pazimene 
mukunenazi. 

19. Ndipo aulendo adadza 
(pafupi ndi chitsimecho) Ndipo 
adatuma wotunga madzi wawo, 
Choncho iye adaponya ndowa 
yake (Mchitsime, ndipo akukoka 
ndowa ija Adaona mwana) nati: 
"Eee, chisangalalo Changa! Aka 
kamwana kakamuna! Pomwepo 
Iwo (amene adalipo pachitsimepo) 
Adambisa kwa apaulendo anzawo) 
monga Katundu wamalonda 
(yemwe adamgula). Koma 
Mulungu ankadziwa zimene adali 
Kuchita (ndipo adanka naye ku 
Iguputo). 1 












19-20. Apa tikuona kuti kugulitsana anthu kudayambika kalekale zedi 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



489 



^r tjA-i 



^ Y ci~*»jj ^J-** 



20. Ndipo adamgulitsa 
pamtengo wochepa Ndi ndalama 
zapang'ono, zowerengeka (Poopa 
kuti angawadzere eni Mwanayo). 
Ndipo sadalabadire za iye. 

21. Ndipo uja (amene) 
adamgula ku Iguputo, Adati kwa 
mkazi wake: "Mkonzere pokhala 
Pabwino (kapolo uyu): mwina 
angatithandize Kapena 
tingamsandutse kukhala mwana 
(wathu)." Motero tidamkhazika 
Yusuf m'dziko (La Iguputo 
mwachisangalalo), ndi kuti 
Timphunzitse kumasulira nkhani 
(zamaloto). Ndipo Mulungu 
Ngopambana pa zinthu Zake 
(zimene Wafuna kuti zichitike); 
koma anthu Ambiri sadziwa. 

22. Ndipo pamene (Yusuf) 
adafika pa msinkhu, Wodzindikira 
zinthu tidampatsa kuweruza ndi 
Nzeru. Umo ndi momwe 
timawalipirira ochita Zabwino. 

23. Ndipo mkazi uja yemwe 
m'nyumba mwake Mudali iye 
adamlakalaka (Yusuf) Popanda iye 
kufuna. Ndipo (mkaziyo) Adatseka 
makomo, nati: "Bwera kuno." 
(Yusuf) adati: "Ndikudzitchinjiriza 









©, 



&»» 









(il^l 



't^t^*^i^3vaU 



*&w)2m 



kuyambira zaka 4,000 zapitazo chipembedzo cha Chisilamu chisanadze, 
chomwe chidaza ndi Mtumiki Muhammad(SAW). Koma adani achipembedzo 
cha Chisilamu akuchinamizira kuti ndicho chidadza ndi ukapolo wogulitsa 
anthu. Chikhalirecho Chisilamu ndicho chidadza kuzalimbikitsa zopereka ufulu 
kwa kapolo. 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



490 



>t ftjfcl 



\ t <Ji-*»jj ^J-** 



Ndi Mulungu (kuchita tchimolo). 
Ndithu iye (Mwamuna wako) ndi 
bwana wanga. Wandikonzera 
bwino pokhala panga (M'nyumba 
mwakemu, ndipo sindichita 
Chinyengo chotere). Ndithu, 
achinyengo Siziwayendera bwino." 

24. Ndipo (mkaziyo) adaikira 
mtima pa iye (Kuti achite naye 
kanthu) ndipo naye (Yusuf) 
adaikira mtima pa iye (kuti 
Ammenye). Pakadapanda kuona 
chisonyezo Cha Mbuye wake 
(chakumzindikiritsa kuti Asatero, 
akadammenya. Koma adamthawa). 
Tidachita izi kuti timchotsere 
chinthu Choipa ndi chauve; 
ndithudi, iye adali Mmodzi mwa 
akapolo athu oyeretsedwa. * 

25. Ndipo (onse awiri) 
adathamangitsana Kukhomo (uku 
Yusuf akuthawa) ndipo (Mkaziyo) 
adang'amba mkanjo wake 
Chakumbuyo. Ndipo mwamuna 
wake Adampezerera pakhomo; 
mkaziyo adati (Kwa mwamuna 
wake mwaugogodi): "Palibe 



> <.. ' ' * ?' '. f\ ' 






(r^l C> loo I {£***&} 



1 Musamchitire choipa amene wakuchitirani chabwino, ngakhalenso amene 
wakuchitrani choipa kumene. Makamaka amene sadakuchitireni choipa (ndiye 
chisimu). Koma alipo anthu ena oipitsitsa zedi amene amachitira zoipa yemwe 
akuwachitira zabwino. Anthu otero ngoipitsitsa kuposa nyama zamtchire, 
ndipo oterewa Mulungu adzawakhaulitsa koopsa. Ndipo machitidwe okhala 
mwamuna ndi mkazi kuseri kwaokha ngoletsedwa M'shariya ya chisilamu 
chifukwa mwamuna kukhala ndi mkazi amene sali mnyazi wake 
kumalakwitsa. Msati awa ndi alamu ndikhoza kukhala nawo pawokha. 
Kukhala ndi mlamu wako kuseri, ndi ngozi imeneyo! 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



491 



U *>i 



1 Y ci-*»jj Sjj—' 



Mphoto kwa yemwe akufuna 
kuchita Choipa ndi mkazi wako 
koma kumponya Kundende, 
kapena kupatsidwa chilango 
Chowawa." 

26. (Yusuf) adati (podziteteza): 
"(Mkazi) Uyu ndi yemwe 
wandifuna popanda ine 
Kumufuna." Ndipo mboni 
yochokera ku Banja la mkaziyo 
idaikira umboni; (Idati): "Ngati 
mkanjo wake wang'ambidwa Cha 
kutsogolo,ndiye kuti( mkazi uyu) 
akunena zoona, Ndipo iye (Yusuf) 
ndi Mmodzi mwa onena zabodza. 

27. Koma ngati mkanjo wake 
wang'ambidwa Chakumbuyo 
ndiye kuti (mkazi uyu) wanena 
Bodza ndipo iye (Yusuf) ndi 
m'modzi mwa onena Zoona. 

28. Choncho (mwamuna uja) 
pamene adaona Mkanjo wake (wa 
Yusuf) utang'ambidwa 
Chakumbuyo, (adadziwa kuti 
Yusuf ndi Amene amafuna 
kugwirilidwa), Adati: "Ndithudi, 
izi ndi ndale zanu akazi. Ndithu, 
ndale zanu ndi zazikulu (Iwe 
mkazi wanga ndi amene 
udatsimikiza Kuchita choipa ndi 
m'nyamatayu)." 

29. "Yusuf! Zipewe izi 
(usauze aliyense). Ndipo (iwe 
mkazi) Pempha chikhululuko ku 






Oo OJs^^ (itfO^ <*>&$ {^XfiJh 









Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



492 



>T frjA-i 



^ T UL*ijj 5jj-»» 



tchimo lako, Ndithu, iwe ndiwe 
mmodzi mwa olakwa!" 

30. Ndipo akazi a mu 
mzindamo (ataimva Nkhaniyi) 
anati: "Mkazi wa nduna 
Akulakalaka m'nyamata wake 
popanda Kulakalakidwa ndi iye; 
ndithu, Chikondi chamufooketsa 
zedi; ndithudi, Ife tikumuona 
(mkaziyu kuti) ali Mkusokera 
koonekera." 

31. Ndipo (mkazi wa nduna) 
pamene adamva Kunyogodola 
kwawo, adawaitana (kuti Adzaone 
kukongola kwa Yusuf kuti adziwe 
Kuti wathedwa nzeru polakalaka 
Yusuf Ngosayenera 
kudzudzulidwa). Ndipo 
Adawakonzera phwando 
ndikupatsa Aliyense wa iwo 
mpeni; kenaka adamuuza (Yusuf): 
"Tuluka ndi kubwera pamaso Pa 
iwo." Choncho pamene (akazi aja) 
Adamuona, adaona kuti nchinthu 
chachikulu zedi ndipo adadzicheka 
manja awo (Ndi mipeni ija. 
Sadazindikire kuti Akudzicheka 
chifukwa cha chidwi ndi 
Kukongola kwa Yusuf), Ndipo 
adati, "Hasha Lillah! 
(tikudzitchinjiriza kwa Mulungu) 
uyu simunthu, uyu Sichina koma 
ndi mngelo wolemekezeka." 

32. (Mkazi wa nduna) adati: 
"Uyu ndi amene 









m&fitej$ti*& 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



493 



>y %}kr\ 



\ y Ulsjj djj-«» 



Mumandidzudzula naye. Ndithudi 
ndidamulakalaka pomwe iye 
samandifuna ndipo Anadziteteza. 
Ndipo ngati sachita Chimene 
ndikumulamula, ndithu 
Amangidwa ndipo ndithu, akhala 
m'gulu La onyozeka!" 

33. (Yusuf) adati: "E Mbuye 
wanga! Ndende ndi yabwino kwa 
ine Kuposa izi akundiitanira. Ngati 
simundichotsera ndale Zawo ndiye 
kuti Ndiwacheukira ndikukhala 
Mmodzi mwa mbuli." 1 

34. Ndipo Mbuye wake 
Adamuyankha (pempho Lake) 
ndikumchotsera ndale zawo. 
Ndithudi, Iye Ngwakumva, 
Ngodziwa. 

35. Kenako kudaoneka kwa 
iwo, (nduna ndi Anthu ake) 
pambuyo poona zizindikiro (Zonse 
zakuyeretsedwa kwa Yusuf) kuti 
Akamponye kundende kwa Nthawi 
yochepa (pofuna kumusungira 
Ulemu mkazi wa nduna). 

36. Ndipo anyamata awiri 
adalowa m'ndende Pamodzi ndi 
iye. M'modzi mwa iwo adati 
(Kumuuza Yusuf): "Ndithu, ine 
ndalota Ndikufulula mowa." Ndipo 






'^l&S&pf ™'* 












1 Akazi aja atamuona Yusuf tsiku limenelo nawonso anadzazidwa ndi chikondi 
chachikulu nayamba kumtumizira mithenga ndi makalata. Ndipo Yusuf 
adaganiza kuti ndibwino angopita kundende poopa kuti akaziwo 
angamulakwitse. 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



494 



^T *>i 



^ t *-A-*»jj *j>^ 



wina adati: "Ndithu ine ndalota 
ndikusenza mikate Pamutu panga 
yomwe idali kudyedwa ndi 
Mbalame." "Tiuze tanthauzo lake. 
Ndithu, ife tikukuona iwe kuti 
ndiwe Mmodzi wa anthu abwino". 

37. (Yusuf) adati: "(Kupyolera 
mu uneneri Umene ndapatsidwa 
ndingathe kukumasulirani Maloto 
anuwa ndi zinthu zina Zobisika 
kwa inu), sichikudzerani Chakudya 
cha mtundu uliwonse choti 
Mungapatsidwe koma ndikhala 
Nditakumasulirani tanthauzo lake 
chisanakufikeni; (Ngati 
mukufunadi ndikuchitirani 
zimenezi). Izi ndi zina mwa 
zomwe Mbuye wanga 
Wandiphunzitsa. Ndithudi, ine 
ndasiya Njira za anthu 
osakhulupirira Mulungu Ndiponso 
omwe akukana za tsiku la 
Chimaliziro." 

38. "Ndipo ine ndatsata 
chipembedzo cha makolo anga 
Ibrahim, Isihaka ndi Yakubu; 
ndipo Sikudali koyenera kwa ife 
kumphatikiza Mulungu ndi 
chilichonse. (Ndipo Kuzindikira) 
zimenezi ndi ubwino Wa Mulungu 
umene uli paife ndi anthu ena. 
Koma anthu ambiri sathokoza." 

39. "E inu anzanga awiri 
am'ndende! Kodi milungu 
Yambiri yosiyana ndiyo yabwino 



e ^<y^ft)£& 






% ^ W»«J WoV- V»5*S5 






Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



495 



U 9,£r\ 



\ y Ul*ijj ^jj-j 



(Kupembedzedwa), kapena 
Mulungu mmodzi Mwini 
mphamvu (pachilichonse)?" 

40. "Simupembedza china 
kusiya lye (Mulungu) Koma ndi 
maina basi amene inu nokha 
Mudawatcha ndi makolo anu, 
Mulungu Sadatsitse umboni 
uliwonse Pazimenezo. Palibe 
lamulo lina koma Ndi la Mulungu 
basi. Walamula kuti 
Musampembedze aliyense koma 
lye basi. Chimenecho ndicho 
chipembedzo choongoka, Koma 
anthu ambiri sadziwa (monga inu 
Mulili popembedza mafano)." 

41. E inu anzanga awiri 
am'ndende! Tsono Mmodzi wainu 
(abwerera kuntchito yake) 
Azikamwetsa mowa bwana wake 
(monga Zidalili poyamba);koma 
winayo Aphedwa mopachikidwa, 
ndipo mbalame Zidzadya mutu 
wake. Chiweruzo chaweruzidwa 
Kale (kwa Farawo) pa chinthu 
Chomwe mudali kufunsa." 

42. Ndipo (Yusuf) adauza 
yemwe adamdziwa kuti 
Apulumuka mwa awiri wo: 
"Ukandikumbuke Ponditchula 
pamaso pa Mbuye wako (Farawo; 
Ukamuuze kuti ndamangidwa 
popanda tchimo)." Koma Satana 
adamuiwalitsa kumkumbutsa 
Mbuye wake. Tero (mneneri 


















Siirat 12. Yusuf 



Juzu 12 



496 



\r f-jir\ 



} Y *-A-*»jJ OjJ-*' 



Yusuf) adakhala M'ndende zaka 
zingapo. 

43. Ndipo (tsiku Una) mfumu 
(Farawo adalota) Nati (kwa nduna 
zake): "Ndithudi, ine Ndalota 
ng'ombe zisanu ndi ziwiri 
Zonenepa zikudyedwa ndi 
ng'ombe zisanu Ndi ziwiri 
zowonda ndiponso ndalota Ngala 
zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina 
(Zisanu ndi ziwiri ) zouma. E inu 
Akuluakulu! Ndimasulireni maloto 
Angawa, ngati inu mumatha 
kumasulira maloto." 

44. (Iwo) adati: "Amenewa ndi 
maloto Osakanikirana (simaloto 
omveka)! Ndipo Ife sitili odziwa 
kumasulira maloto Amtundu 
umenewu." 

45. Pamenepo amene 
adapulumuka mwa awiri Aja 
adanena atakumbukira (pempho la 
Yusuf) patapita nyengo (yaitali), 
Adati: "Ine ndikuuzani tanthauzo 
Lake. Choncho nditumeni (kuti 
ndikakufunireni tanthauzo lake)." 

46. (Adanka kundende 
ndikumpempha Yusuf 
Chikhululuko chifukwa cha 
kuiwala kwake. Ndipo adati): 
"Yusuf! E iwe woona! Tiuze za 
ng'ombe zisanu ndi ziwiri 
Zonenepa zikudyedwa ndi zisanu 
ndi Ziwiri zoonda, ndi ngala zisanu 









taw®* 



•' 









f- »L* " 



1£" 






Surat 12. Yusuf 



Juzu 12 



497 



\y *>i 



s y ci-^ji &jy 



ndi Ziwiri zaziwisi ndi zina 
zouma; kuti Ine ndibwerere kwa 
anthu kuti akadziwe." 

47. (Yusuf) adati: "Mudzalima 
zaka zisanu Ndi ziwiri 
mondondozana ndi mwakhama 
Ndipo zimene mwakolola Zisiyeni 
m'ngala zake, kupatula zochepa 
Zimene muzidzadya (kuti 
zam'ngalazo Mudzadye mzaka 
zanjala). 

48. "Kenako pambuyo pake 
Zidzadza zaka Zisanu ndi ziwiri za 
Masautso zomwe zidzadya Zimene 
mudasunga m'mbuyo Kupatula 
zochepa zimene muzidzazisunga 
(Mobisa kuti zidzakhale mbewu.) 

49. "Kenako pambuyo pa izi 
chidzadza chaka Chomwe anthu 
m'menemo adzapulumutsidwa 
(Ndi Mulungu). Ndipo m'menemo 
adzafinya (Zakumwa)." 

50. Ndipo mfumu idati : 
"M'bweretseni lye kwa ine." 
Koma pamene mthenga (wa 
Mfumu) adamfika (Yusuf, iye) 
adati: "Bwerera kwa Mbuye wako 
ndipo Ukamfunse nkhani ya akazi 
omwe Ankadzicheka manja awo. 
Ndithu, Mbuye wanga akudziwa 
bwino ndale Zawo. (Koma 
ndikufuna mfumu kuti Idziwe za 
kuyera kwanga kuti Andiyeretsere 
maganizo ndipo asandiope)." 






%ys®&$&%tiSQ 



'''"*&& 












Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



498 



>r *jk\ 



\ V U1~»»JJ *J>^ 



51. (Mfumu idasonkhanitsa 
akazi aja ndipo) idati: "Kodi 
nkhani yanu njotani pamene 
Mudamulakalaka Yusuf Pomwe 
iye asakufuna?" Adati: "Hasha 
Lillah! (tikudzitchinjiriza kwa 
Mulungu) Ife sitidadziwe choipa 
chilichonse kwa iye. (Tidayesayesa 
kuti achite nafe Choipa koma 
sadalole)." (Nayenso) mkazi wa 
nduna adati: "Tsopano choonadi 
chatsimikizika; ine Ndine amene 
ndidamulakalaka iye Asakufuna. 
Ndithu, iye ndi mmodzi mwa Oona." 

52. (Yusuf adati): "Zimenezo 
(zofuna kuti Afunsidwe chonchi) 
n'chifukwa chakuti (Nduna) 
idziwe kuti ine sindidaichitire 
Zoipa iyo kulibe, ndikuti Mulungu 
saongolera ndale za anthu 
Achinyengo (kuti ipambane). 

53. "Ndipo ine sindikuyeretsa 
mtima wanga. Ndithu, mtima 
uliwonse umalamulira kwambiri 
Ku zoipa kupatula umene Mbuye 
wanga wauchitira chifundo. 
Ndithudi, Mbuye Wanga 
Ngokhululuka, Ngwachisoni. 

54. Choncho Mfumu idati: 
"Mubwere naye kwa ine kuti ine 
Mwini ndimsankhe." Ndipo 
pamene adalankhula naye (mfumu) 
Idati: "Ndithu, iwe lero kwa ife 
Wakhala wolemekezeka, 
Wokhulupirika" 















Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



499 hr,j*-i 



\ t UL*>ji $jj-» 



55. (Yusuf) adati: "Ndiikeni 
kukhala Muyang'aniri wankhokwe 
zazinthu Zam'dziko lonse. 
Ndithudi, ine ndine Msungi 
wodziwa." 

56. Ndipo motero tidampatsa 
ulemerero Yusuf M'dziko (la 
Iguputo); amakhala M'menemo 
paliponse pamene wafuna. 
Timam'bweretsera chifundo 
Chathu Amene tamfuna, ndipo 
sitisokoneza Malipiro a ochita 
zabwino. 

57. Ndithudi malipiro a tsiku la 
chimaliziro Ngabwino zedi kwa 
amene akhulupirira Ndi 
kumamuopa (Mulungu). 

58. Ndipo adadza abale ake a 
Yusuf (kukafuna Chakudya 
kumeneko pamene ku Middle East 
kudagwa chilala chadzaoneni) Ndi 
kulowa kwa iye ndipo (iye) 
Adawazindikira pomwe iwo 
sankamzindikira. 

59. Ndipo pamene 
adawakonzera chakudya chawo, 
Adati: ("Ngati mudzabwereranso 
kachiwiri) Mudzabwere ndi m'bale 
wanu wa kumbali Ya bambo anu, 
kodi simuona kuti ine 
Ndikukwaniritsa muyeso, ndipo 
ndine Wabwino kwambiri 
polandira (alendo)?" 



S&®J&ffiftS&& 



®: 



9>\' 



Sir 















@ a^^i 



Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



500 



>r tjJ-i 



^ y c-a-jjj ^j^*' 



60. "Komangati 
simudzandibweretsera iye, 
Simudzakhala ndi mulingo 
(Wachakudya) kwa ine, ndipo 
Musadzandiyandikire." 

61. (I wo) adati: "Tikayetsetsa 
kuwanyengerera Bambo wake za 
iye (kufikira Akatipatse). Ndithu, 
ife tikachita Zimenezi." 

62. Ndipo (Yusuf) adati kwa 
anyamata ake a ntchito: "Ikani 
chuma chawo m'mitolo Yawo kuti 
akachizindikire akabwerera Ku 
mawanja awo. (Tinkachita izi) 
Mwina angabwererenso (kuno)." 

63. Ndipo pamene adabwerera 
kwa bambo wawo, Adati: "E 
Bambo wathu ! Tikamanidwa 
Muyeso wachakudya (paulendo 
wachiwiri Pokhapokha titsagane 
ndi m'bale wathuyu). Choncho 
mtumizeni m'bale wathu pamodzi 
Ndi ife kuti akatipimire (mlingo 
Wokwana); ndithu, ife 
tikamsunga." 

64. (Yakubu) adati: "Kodi 
ndingakukhulupirireni Pa iye 
kuposa momwe 

Ndidakukhulupirirani pa m'bale 
wake Kale (yemwe 
mudamsokeretsa)? Koma Mulungu 
ndi Yemwe ali wabwino posunga, 
Ndipo Iye Ngwachifundo kuposa 
Achifundo onse. 












Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



501 



\T *>1 



^ T ci-*»jj ^jj- - 



65. Ndipo pamene adatsekula 
katundu wawo, Adapeza chuma 
chawo chabwezedwa kwa Iwo. 
Adati: "E, Bambo wathu! 
Tingafunenso chiyani (kwa 
munthu Waufuluyu)? Ichi chuma 
chathu Chabwezedwa kwa ife; 
ndipo tikabweretsa chakudya 
chothandizira mawanja athu; 
Ndipo m'bale wathu tikamsunga; 
Tikapezanso muyeso wangamira 
imodzi Yoonjezera. Umenewu ndi 
mlingo Wochepa(kwa mfumu ya 
ufuluyo). 

66. (Yakubu) adati: 
"Sindingamtumize Pamodzi ndi 
inu pokhapokha mundipatse 
Lonjezo m'dzina la Mulungu kuti 
ndithudi Mudzambweza kwa ine 
pokhapokha Nonsenu 
mutazingidwa (ndi zoopsa). Ndipo 
pamene adapereka lonjezo lawo, 
(lye) adati: "Mulung ndiye 
Muyang'aniri (mboni) pazimene 
tikunenazi." 

67. Adatinso: "E inu Ana anga! 
Musakalowe (mu Iguputo) 
Pachipata chimodzi koma 
kaloweni Pazipata zosiyanasiyana. 
Ndipo Sindingakuthandizeni 
chilichonse Kwa Mulungu. 
Lamulo ndi la Mulungu Basi; kwa 
lye ndiko ndatsamira; ndipo 
Otsamira atsamire kwa lye." 












yi 



®6%J$\$j&&j 



Surat 12. Yiisuf 



Juzu 13 



502 



>r *>i 



\ T <-i-»ji ^J*** 



68. Ndipo pamene adalowa 
monga momwe Bambo Wawo 
adawalamulira, sikudawathandize 
Chilichonse kwa Mulungu 
kupatula Khumbo lomwe lidali 
mumtima mwa Yakubu 

(Ndi lomwe) adalikwaniritsa 
(Yakubu Adali kufuna Yusuf ndi 
m'bale Wake akumane mwamseri; 
ndipo Adakumanadi). Ndithu iye 
(Yakubu) Adali wanzeru chifukwa 
chakuti Tidamphunzitsa. Koma 
anthu ambiri Sadziwa. 

69. Ndipo pamene adalowa kwa 
Yusuf (Ndikumuona m'bale wake 
atalowa Payekha), adamkumbatira 
m'bale wakeyo Nati: "Ndithu, ine 
ndine m'bale Wako; choncho 
usadandaule pazimene (Abale 
athu) akhala akuchita." 

70. Ndipo pamene 
adawakonzera chakudya Chawo, 
adaika chikho chomwera madzi 
Mumtolo wa m'bale wakeyo. 
Kenako Woitana adaitana: "E inu 
apaulendo! Inu ndinu anthu akuba. 

71. (Onse abale ake a Yusuf) 
pamene Adawacheukira, adati: 
"Kodi Mukusowa chiyani?" 

72. Adati: "Tikusowa muyeso 
wa Mfumu; Ndipo amene 
aubweretse, alandira Mtolo 
wangamira yathunthu; (ndipo 
Mneneri Yusuf adati): "Ndipo ine 
Ndine muimiriri pa zimenezi." 












Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



503 



ir *>i 



) T ci-^JJ 6jJ**> 



73. (Iwo) adati: "Tikulumbirira 
pali Mulungu! Ndithu, inu 
mukudziwa Kuti sitidadze 
kudzaononga mdziko, Ndiponso 
sitili akuba." 

74. Adati: "Mphoto (chilango) 
yake Ikhala yotani ngati Mukunena 
bodza?" 

75. Adati: "Mphoto yake ndi 
yemwe (Chikhocho) chapezeka 
mumtolo wake, lye ndiye mphoto 
yake. (Agwidwe Monga kapolo 
kwa chaka chimodzi)". Umu ndi 
momwe timawalipirira anthu 
Achinyengo. 

76. Ndipo (mneneri Yusuf) 
adayamba Kufufuza m'mitolo 
mwawo asanafufuze Mumtolo wa 
m'bale wake; kenako 
Adachitulutsa mumtolo wa m'bale 
wake. Umu ndi momwe 
tidamlinganizira ndale Yusuf (kuti 
ampeze m'bale wake). 
Mwachilamulo cha mfumu (ya 
m'dzikolo) Sakadamutenga m'bale 
wake (monga kapolo) Koma 
mmene Mulungu adafunira 
(powaonetsaAbale ake za 
chilamulo cha kwawo chomuika 
Mu ukapolo munthu wakuba). 
Timawakwezera Paulemerero 
amene tawafuna.Ndipo pa 
wodziwa Aliyense pali 
wodziwanso kuposa iye. 












Siirat 12. Yusuf 



Juzu 13 



504 



>T frjA-i 



\ Y <-i-»ji *j>"' 



77. (I wo) adati: "Ngati waba, 
m'bale Wakenso adabapo kale." 
(Uku kudali Kumunamizira Yusuf 
bodza pomwe iwo Sankadziwa 
kuti yemwe akuyankhula Nayeyo 
ndiye Yusuf). Koma Yusuf 
Adabisa (mawu awa) mumtima 
mwake, (Chifukwa chowamvera 
chisoni) ndipo Sadawaululire. 
Adati: "Inu muli ndi Chikhalidwe 
choipa ndipo Mulungu akudziwa 
Zomwe mukunena!" 

78. (Iwo) adati: "E inu bwana! 
Uyu ali ndi Bambo wake 
wokalamba Kwambiri; choncho 
Tengani mmodzi wa ife mmalo 
mwake; Ndithudi, ife tikuona kuti 
inu ndinu Mmodzi mwa ochita 
zabwino". 

79. (Yusuf) adati: "Ha! 
tikudzitchinjiriza Mwa Mulungu, 
sitingagwire wina koma Yemwe 
chuma chathu tachipeza ndi iye, 
Kuopa kuti tingakhale ochita zoipa. 

80. Choncho, pamene adataya 
mtima za iye, Adapita pambali 
kukanong'onezana. Wamkulu 
wawo adati: "Kodi simudziwa Kuti 
Bambo wanu adatenga lonjezo 
Kuchokera kwa inu m'dzina la 
Mulungu (Kuti mudzambweza 
iyeyo?) Ndiponso Kale mudalakwa 
(pamapangano anu) pa Za Yusuf. 
Choncho sindichoka dziko Lino 
kufikira atandilola Bambo 















Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



505 ir*j*-i 



^ t <-A-«»ji ^jj- - 



(kutero) kapena Mulungu 
andilamule (zondichotsa kuno 
Pomasulidwa m'bale wangayu); 
lye Ngwabwino Polamula kuposa 
olamula. 

81. "Bwererani kwa abambo 
anu ndipo mukawauze (Kuti): "E 
Bambo wathu! Ndithu mwana 
wanu Adaba. Ndipo ife sitidaikire 
umboni (Wakuti wakuba 
achitidwe ukapolo) Koma 
pazomwe tidazidziwa (kuti mwaife 
Mulibe wakuba), ndipo sitidali 
Kudziwa zamseri." 

82. "Ndipo afunseni anthu A 
m'mudzi mom we Tidalimo ndi 
apaulendo Omwe tadza 
nawo,ndipo Ndithudi ife tikunena 
zoona." 

83. (Yakubu) adati: "Koma 
mitima yanu Yakukometserani 
chinthu. (Kwa ine Ndi) kupirira 
kwabwino kokha basi. Mwina 
Mulungu adzandibweretsera Onse 
pamodzi. Ndithudi, lye Ngodziwa, 
Ngwanzeru zakuya." 

84. Ndipo adawachokera 
ndikunena (Kuti): "Ha! 
kudandaula kwanga za Yusuf!" 
Ndipo maso ake adayera Chifukwa 
cha kudandaula ndipo iye 
Adadzadzidwa ndi chisoni. 

85. (Iwo) adati: "Pali Mulungu! 
Simusiya kumkumbukira Yusuf 












Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



506 



>r sjA-i 



^ T *-A-»*Ji *JJ-*' 



(Ndikulira) mpaka mufika 
podwala, Kapena mukhale mwa 
owonongeka (ndi Imfa)." 

86. (lye) adati: "Ndithu, ine 
ndikusuma Dandaulo langa ndi 
kukhumata kwanga Kwa Mulungu, 
ndipo ndikudziwa Kupyolera mwa 
Mulungu zomwe Simukudziwa." 

87. "E ana anga! Pitani 
mukafufuzefufuze Za Yusuf ndi 
mbale wake, ndipo Musataye 
mtima pa chifundo cha Mulungu. 
Ndithu, palibe amene amataya 
Mtima za chifundo cha Mulungu 
koma Anthu osakhulupirira." 

88. (Ndipo adapita ku Iguputo). 
Choncho Pamene adalowa kwa iye 
(Yusuf) adati: "E inu 
olemekezeka! Masautso 
Atikhudza, ife ndi maanja athu; 
Choncho tabwera ndi chuma 
chopanda Pake. Tidzadzireni 
mlingo (ngakhale Chuma 
chathucho chili chopanda pake), 
Ndipo tichitireni zaufulu. Ndithu 
Mulungu Amalipira ochita 
zaufulu." 

89. (Iye) adati: "Kodi 
mukudziwa zomwe Mudamchitira 
Yusuf ndi m'bale wake Pamene 
inu mudali mu umbuli?" 

90. (Iwo) adati: "Kodi iwe 
ndi we Yusuf?" Adati: "Ine ndine 
Yusuf, ndipo uyu Ndi m'bale 












Surat 12. Yusuf Juzu 13 I 507 I > r *>» 



\ t U^**jt ^jj** 



wanga; Mulungu watichitira 
Zabwino. Ndithu, amene aopa 
Mulungu Ndikumapirira, 
(Mulungu amulipira). Ndithu, 
Mulungu sasokoneza malipiro 
Aochita zabwino." 

91. (Iwo) adati: "Pali Mulungu! 
Mulungu Wakusankha pa ife, 
ndipo ife tidalidi Olakwa." 

92. (lye) adati: "Lero palibe 
kukudzudzulani; Mulungu 
akukhulukirani, Ndipo lye 
Ngwachifundo chochuluka Kuposa 
achifundo." 

93. "Pitani ndi mkanjo wangawu 
ndipo Mukauponye pamaso pa 
Bambo wanga Ndipo iwo akapenya. 
Kenako nonsenu Ndi mawanja anu 
onse mudze kwa ine." 

94. Ndipo aulendo pamene 
adamuka (Kubwerera kwawo). 
Bambo wawo (Yemwe adali ku 
Sham) adati: "Ndikumva fungo la 
Yusuf pakadapanda Kuti muli ndi 
chikhulupiriro choti 
Ndasokonezeka nzeru, 
(mukadandikhulupirira.") 

95. (Iwo) adati: "Pali Mulungu! 
Ndithu Muli mkusokera kwanu kwa 
kale (Pokonda Yusuf kuposa ife)." 

96. Choncho pamene adadza 
wotenga nkhani Yabwino, 
adauponya (mkanjo wa Yusuf) 















Surat 12. Yiisuf 



Juzu 13 



508 



IT frj*-i 



^ T ei— »jj ^jj-*' 



Patsogolo pankhope yake, ndipo 
Pompo adapenya. Adati: "Kodi 
Sindinakuuzeni kuti ine 
ndikudziwa Kupyolera mwa 
Mulungu zomwe inu 
Simukuzidziwa?" 

97. (Iwo) adati, "E Bambo 
wathu! Tipemphereni chikhululuko 
pa Machimo athu. Ndithu ife 
tidali Olakwa." 

98. (lye) adati: "Posachedwapa 
(ndikamuona Yusuf) 
ndikupempherani chikhululuko 
Kwa Mbuye wanga. Ndithu, lye 
NgokhululukaZedi, Ngwachisoni." 

99. Ndipo pamene adalowa 
Kwa Yusuf, adawakumbatira 
Makolo ake ndikunena: "Lowani 
mu Iguputo, Insha'llah, (Mulungu 
akalola) Mwamtendere." 

100. Ndipo (pamene adafika 
kwa Yusuf),(Iye) adawakweza 
Makolo ake ndi kuwaika 
pampando (wake) wachifumu, 
Ndipo onse adagwa kumlambira 
(monga Mwachizolowezi chawo 
nthawi imeneyo). Ndipo (Yusuf) 
Adati: "E inu Bambo wanga! Hi 
ndilo tanthauzo (lenileni) La 
maloto anga akale. Palibe 
chipeneko Mbuye wanga 
Wawatsimikiza (maloto wo). Ndipo 
adandichitira Zabwino 
ponditulutsa kundende ndi 



®6J^<Mt6^1 












Surat 12. Yusuf 



Juzu 13 



509 



\T *j*-l 



^ t *-i~»»jj *j>- , > 



pokubweretsani Inu kuchokera 
kuchipululu, pambuyo 
pokhwirizira (Chidani) Satana 
pakati pa ine ndi abale anga. 
Ndithudi Mbuye wanga amadziwa 
kwambiri chinsinsi cha zomwe 
Wakonza kuti zichitike. Ndithu, 
lye Ngodziwa, Ngwanzeru. 

101. (Kenako adathokoza ndi 
kupempha Mulungu kuti): "E 
Mbuye wanga! Ndithu, 
Mwandipatsako ufumu ndi 
kundiphunzitsako Kumasulira 
nkhani (zamaloto). E, inu Mlengi 
wa thambo ndi nthaka. Inu ndiye 
Mtetezi wanga padziko Lapansi 
ndi tsiku la chimaliziro. (Ndipo 
Nthawi ya imfa yanga) 
mudzandipatse imfa Ndili 
Msilamu ndipo kandikumanitseni 
ndi Ochita zabwino." 

102. Izi ndi zina mwankhani 
zamseri (Zomwe) tikukuululira 
iwe. Ndipo siudali nawo pamodzi 
Pamene adatsimika chochita 
Chawo (uku) akuchita chiwembu 
(Chawo) choipa. 

103. Ndipo ambiri mwa Anthu 
sakhulupirira Ngakhale utalimbika 
chotani. 

104. Ndipo sukuwapempha 
malipiro Pazimenezi. Sichina izi 
(zimene Wadza nazo),koma ndi 
ulaliki kwa Zolengedwa zonse. 









Surat 12. Yiisuf 



Juzu 13 



510 



\T t>i 



^ t <*jL»»ji *jj-^ 



u*3^]3dP(^fe 

/T}> ^ 9 A 9?Y*' 99 'X'9**' S 9) 'J' 



mjMS&v&z 



j&. 



%&$ 



105. Ndipo ndi zisonyezo 
zingati (zosonyeza Kuti Mulungu 
alipo) kumwamba ndipansi 
Zomwe akuzidutsa pamene iwo 
sakuzilabadira. 1 

106. Ndipo ambiri a iwo 
Sakhulupirira Mulungu Koma 
momphatikiza! 2 

107. Kodi akudziika pachitetezo 
kuti Silingawadzere tsoka 
lachilango Cha Mulungu, kapena 
kuti siingawadzere Kiyama 
mwadzidzidzi pomwe Iwo 
sakuzindikira? 

108. Nena: "Iyi ndi njira yanga. 
Ndikuitanira Kwa Mulungu 
mwanzeru zokwanira,ine ndi Omwe 
akunditsata. Ndithu, Mulungu 
Wapatukana (ndi mbiri zopunguka). 
Ndipo ine sindili mwa ophatikiza 
(Mulungu ndi zinthu zina)." 3 



1 Apa tanthauzo lake nkuti zilipo zisonyezo zambiri zosonyeza kuti Mulungu 
alipo zomwe iwo akuziona ali pamudzi ndiponso akuzidutsa akakhala 
pamaulendo awo monga thambo, nthaka, dzuwa, mwezi, nyenyezi, mapiri ndi 
zina zambiri zododometsa zimene zikupezeka kumwamba ndi pansi. 
Akuziona m'mawa ndi madzulo koma iwo saziganizira. 

2 Apa akutanthauza kuti ambiri a iwo amamphatikiza Mulungu ndi milungu 
yabodza. Iwo amavomereza kuti Mulungu ndiye Mlengi wopatsa zonse. Koma 
kuonjezera pachikhulupiriro choterechi, amapembedzanso mafano. Ndipo 
zoterezi masiku ano zikumachitika ndi Asilamu ena amene amafuulira mizimu 
ya anthu akufa kuti iwathangate pamavuto amene awagwera, komwe 
nkumuphatikiza Mulungu ndi mizimu ya anthu akufa. 

3 Apa Mtumiki (SAW) akuuzidwa kuti awauze anthu kuti iye pamodzi ndi 
amene akumutsata kuti amalalikira Chisilamu kwa anthu popereka kwa anthuwo 
mitsutso yanzeru, ndikuperekanso zisonyezo ndi maumboni amphamvu. 
Sibwino Msilamu kutsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino. Qur'an 
ikunenetsa kuti osatsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino 
pokhapokha chinthucho chitanenedwa ndi Mulungu pena Mtumiki Wake. 



i < • ?jx. , . ^ wit, 9 \c 9 k \<"\ 



Siirat 12. Yusuf 



Juzu 13 



511 



ST *jA-1 



^ t Ul*>jj *_)j~* 



109. Ndipo sitidatume 
(Mtumiki aliyense) Patsogolo pako 
koma adali amunaamene 
Tidawavumbulutsira 
(chivumbulutso); ochokera mwa 
Anthu am'midzi. Kodi sadayende 
(iwo Osakhulupirira) pa dziko 
nkuona momwe Mathero a oipa 
omwe adalipo patsogolo Pawo 
(momwe adalili)? Ndipo nyumba 
ya Tsiku la chimaliziro njabwino 
kwa oopa Mulungu. Kodi mulibe 
nzeru? 

110. Mpaka pamene atumiki 
adataya mtima (za Anthu awo) 
nkuganiza kuti Ayesedwa 
onama,chithandizo chathu 
Chidawadzera, ndipo amene 
tidawafuna Adapulumuka. Koma 
chilango chathu Sichibwezedwa 
kwa anthu Oipa. 

111. Ndithu, m'nkhani zawo 
Izi muli phunziro kwa eni nzeru. 
Simawu Opekedwa, koma ndi 
chitsimikizo cha zomwe Zidalipo 
patsogolo pake (m'mabuku ena a 
Mulungu), ndi kumasulira kwa 
Tsatanetsatane pa chilichonse 
ndiponso chiongoko Ndi mtendere 
kwa anthu okhulupirira. 















Osatsatira chinthu kaamba koti anthu ambiri akuchitsatira kapena kaamba koti 
akuluakulu kapena atsogoleri akuchitsatira. Koma poyamba fufuza kuona 
kwake kwa chinthucho. Ndipo ukapeza kuti nchoona, chitsatire. 
Muziganizira mwa nzeru zanu zonse pachinthu chilichonse chimene 
mukuuzidwa. Kutero ndiko kutsatira zophunzitsa za Qur'an. 



Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



512 



)T *jir\ 



\ T JLP^I 5jj- 




SURAT AR-R'AD XIII 




Sura iyi yayamba ndi nkhani yaikulu yomwe ndi 
kukhulupirira kuti Mulungu alipo. Koma ngakhale zisonyezo 
zolangiza kuti Chauta alipo zikuonekera poyera, Amshirikina 
akukana. Akuikana Qur'an ndi kumkana Mulungu Mwini 
chifundo chambiri. 

Ay a za m'Sura iyi zikutsimikizira za kukwanira kwa 
mphamvu za Mulungu ndi kudodometsa kwa zolengedwa zake, 
monga thambo ndi nthaka, dzuwa ndi mwezi, zomera ndi 
zipatso, ndi zonse zomwe Mulungu adalenga padziko lino 
lophanuka. Ndipo aya za Surayi, zatsimikiziranso za kuuka ku 
imfa ndikuti aliyense adzalipidwa molingana ndi zochita zake. 
Ndipo ayazo zikupitiriza kutsimikizira kuti udindo wakulenga, 
kupereka moyo, imfa, zabwino, mtendere ndi wa Mulungu. 
Kenako Surayi yaponya mafanizo awiri: fanizo la choonadi ndi 
fanizo la chonama pofanizira madzi amene amatsika kumwamba 
ndikuyenda m'zigwa ndi m'makwalala uku atatenga zinyalala 
m'njira mwake. Ndipo thovu limayandama pamwamba pake, 
lomwe lilibe phindu. Ndipo madziwo amatsalira ndi kulowa 
pansi, omwe anthu amathandizidwa nawo. Umo ndi momwe 
chilili choonadi ndi chachabe. Choonadi chimakhazikika ndi 
kupitirira pomwe chachabe sichikhalira kutha ngakhale 
chitakhala ndi mphamvu zotani. 

Kenako aya m' Surayi zafotokoza mbiri za anthu omwe 
adzakhale pamtendere, ndi anthu omwe adzakhale pamasautso. 




Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



513 



1f(>i 



^ T opjJi 5jj~. 



Surat Ar-Ra'd XIII 



\'SMCM. * 



:* 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Alif-Ldm-Mim-Rd. Izi ndi ay a 
za buku ili (lomwe Lasonkhanitsa 
chilichonse Chofunika); ndipo 
chomwe chavumbulutsidwa Kwa 
iwe kuchokera kwa Mbuye wako, 
Nchoonadi; koma anthu ambiri 
Sakhulupirira. 

2. Mulungu ndi Yemwe 
adatukula thambo popanda Mizati 
imene mukuiona; kenako 
adakhazikika Pampando Wake 
wachifumu, (Kukhazikika 
koyenera ndi lye komwe kulibe 
Chofanizira); ndipo adafewetsa 
dzuwa ndi Mwezi (kwa anthu). 
Chilichonse mwa Zimenezi 
chikupitirira kuyenda mpaka 
Nyengo imene idaikidwa. lye ndi 
Yemwe Akuyendetsa zinthu; 
akulongosola aya izi Kuti mukhale 
ndi chitsimikizo pazakukumana 
Ndi Mbuye wanu. 1 

3. Ndipo lye ndiYemwe 
adatambasula nthaka Ndikuika 



Q&#lfe*ijll^ 



%PSS 






\S9* Si S" 



u®^g»A' 



1 Mulungu adafewetsa dzuwa ndi mwezi kuti zitumikire anthu Ake. Chilichonse 
mwa izo chikuyenda molingana ndi chikonzero cha Mulungu kufikira pamene 
lidzathera dziko lapansi. Mulungu ndi Yemwe akuyendetsa zinthu zonse 
zapadziko ndi nzeru Zake zakuya, monga kuzipatsa moyo ndi kuzipatsa imfa 
ndi zina zotere. 

Mulungu akutifotokozera zonsezi kuti tikhale ndi chitsimikizo choti tidzakumana 
Naye pambuyo pa imfa. 



Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 514 I ^ r *>i 



^ r jlp^Ji 6jj-- 



mapiri ndi mitsinje m'menemo. 
Ndipo mtundu uliwonse wazipatso 
Adaupanga m'menemo kukhala 
mitundu Iwiri iwiri, (yachimuna 
ndi yachikazi), Amavindikira usiku 
ndi usana. Ndithu, m'zimenezi 
muli zisonyezo (zazikulu 
Zosonyeza kuti Mulungu alipo) 
kwa Anthu olingalira. 

4. Ndipo m'nthaka muli zigawo 
zogundana, (Koma kumeretsa 
kwake kwa zomera 
Nkosiyanasiyana). Mulinso minda 
Ya mphesa ndi mmera wina ndi 
kanjedza Wokhala ndi nthambi ndi 
wopanda nthambi; (Zonsezi) 
zikuthiriridwa ndi madzi amodzi 
Ofanana, ndipo tikuzichita zina 
kukhala Zabwino kuposa zina 
mkakomedwe kake. Ndithu, 
m'zimenezi muli zisonyezo kwa 
anthu Anzeru. 

5. Ndipo ngati ukudabwa,(basi) 
chodabwitsa Kwambiri ndiko 
kuyankhula kwawo (koti): "Kodi 
tikadzakhala dothi, ndi zoona 
Tidzakhala ndi chilengedwe 
chatsopano? (Mulungu sangathe 
zimenezi)". Iwowo Ndi amene 
sadakhulupirire Mbuye wawo. 
Ndipo kwa iwowo mudzakhala 
magoli M'makosi mwawo; ndipo 
iwo ndi anthu Akumoto, 
m'menemo adzakhala muyaya. 1 












Mulungu akuti chodabwitsa zedi kwa anthu osakhulupirira ndiko kunena 



Siirat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



515 h?*>l \Td*J\ Ijy* 



6. Ndipo akukufulumizitsa kuti 
ubweretse choipa (Chomwe ndi 
chilango chawo) m'malo Mwa 
chabwino; ndithu chikhalirecho 
zilango Zambiri zidapita kale 
(zomwe Akadayenera kuchenjera 
nazo)! Koma Mbuye wako ndi 
mwini chikhululuko kwa Anthu 
pa uchimo wawo. Ndipo ndithu 
Mbuye wako Ngolanga mwaukali. 1 

7. Ndipo osakhulupirira 
akunena: "Bwanji Sichidatsitsidwe 
kwa iye chozizwitsa Chochokera 
kwa Mbuye wake?" Ndithu, Iwe 
ndi we mchenjezi, ndipo mtundu 
uliwonse Wa anthu uli ndi 
muongoli (wakewake yemwe Ali 
ndi njira zakezake zoongolera 
anthuwo, Osati kutsata njira za 
muongoli wina). 

8. Mulungu akudziwa 
chilichonse chimene Mkazi asenza 
(m'mimba mwake) ndi zimene 
Mimba zikupungula ndi zimene 
zikuonjezera. Chinthu chilichonse 
kwa Iye chili ndi Mlingo (wake). 






®&0 






9*2* 



kwawo kwakuti: "Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi, tidzapatsidwanso moyo 
wina watsopano, zidzatheka bwanji zimenezi?" Ndithudi, kukana kwawo za 
kuuka kwa akufa nkododometsa pakuti amene adatha kulenga zinthu 
zikuluzikulu, monga thambo ndi nthaka, mitengo ndi zipatso, nyanja ndi 
mitsinje, ngokhoza kuwabweza pambuyo paimfa yawo. 
1 China chodabwitsa cha anthu osakhulupirira mwa Mulungu ndiko kupempha 
chilango kuti chiwadzere m'malo mopempha zabwino. Iwo ankanena monga 
momwe zilili m'ndime ya 32 m'Surat Anfal kuti: "Ngati izi zimene wadza nazo 
Muhammad (SAW)nzoona zochokera kwa inu (Mulungu), choncho timenyeni ndi 
chimvula chamiyala yochokera kumitambo; kapena chilango china chilichonse 
chopweteka. Koma ife sitimutsatirabe." Umo ndi momwe idalimbira mitima ya 
osakhulupirira. 



Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



516 hr^>i 



y r op^i oj^ 



9. (lye ndi Yemwe ali) 
Wodziwa zamseri Ndi 
zoonekera,Wamkulu, 
Wapamwambamwamba. 

10. Ndi chimodzimodzi (kwa 
lye Mulungu) Amene akubisa liwu 
lake mwa inu ndi Amene 
akulikweza ndi yemwe akudzibisa 
Usiku ndi yemwe akuyenda usana, 
(onse Akuwadziwa). 

11. (Munthu aliyense) ali nalo 
gulu (la Angelo) Patsogolo pake 
ndi pambuyo pake (omwe) 
Amamulondera (ndi kulemba 
zomwe akuchita) Mwa lamulo la 
Mulungu. Ndithudi, Mulungu 
Sasintha zomwe zilipo kwa anthu 
mpaka Atasintha iwo zomwe zili 
m'mitima yawo. Ndipo Mulungu 
akawafunira anthu chilango, Palibe 
chochitsekereza; ndipo alibe 
Mtetezi m'malo mwake 
(Mulungu) 1 

12. lye ndi Yemwe 
amakuonetsani kung'anima 
Mokuopyezani (kuphedwa ndi 
mphezi) Ndi mokupatsani 
chiyembekezo chabwino 
(Chakudza mvula). Ndipo 



®j^%$\?^\jd&\& 












Ukaona anthu zinthu zawo sizikuwayendera bwino, dziwa kuti iwo eni ake 
asintha chikhalidwe chawo chabwino chomwe adali nacho chomwe 
chimawadzetsera madalitso. Munthu akasintha kusiya makhalidwe ake 
abwino, zinthu zake zonse zimaonongeka. Munthu amatchedwa munthu 
akakhala ndi makhalidwe abwino. Koma akaononga makhalidwe ake abwino 
ulemu wake wonse umaonongeka. 



Siirat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



517 



>r fr>» 



\ r op^i ojj- 



amabweretsa Mitambo yolemera 
(ndi madzi amvula). 

13. Ndipo mphezi imalemekeza 
Mulungu Ndi kumthokoza, naonso 
Angelo (Amamlemekeza) 
momuopa. Ndipo Mulungu, 
Amatumiza kumenya kwa mphezi 
ndi Kummenya nako amene 
wamfuna. Ndipo Iwo (Akafiri) 
akutsutsana pa za Mulungu (Kuti 
alipo kapena kulibe pomwe lye 
Alipo). Ndipo lye Ngolanga 
mwaukali. 

14. Kwa lye ndiko kuli 
(kuvomera) pempho Lachoonadi. 
Ndipo aja amene akupempha 
mafano Kusiya lye (Mulungu), 
Sawayankha pachilichonse koma 
(Chikhalidwe chawo) chili ngati 
yemwe Akutambasulira madzi 
manja ake awiri Kuti afike 
m'kamwa mwake; koma 
sangafike. Ndipo mapemphero a 
osakhulupirira sali Kanthu koma 
ndi otaika basi (opita pachabe). 

15. Ndipo amene ali 
kumwamba ndi pansi 
Amamgwadira Mulungu 
Mwachifuniro ndi mopanda 
chifuniro; Ndiponso zithunzi Zawo 
(zimamgwadira) M'mawa ndi 
madzulo. 

16. Nena: "Ndani Mbuye wa 
thambo ndi Nthaka?" Nena: "Ndi 
Mulungu". Nena: 






9 '9? 9S S9 *<t\'±»'\\l'" (< 

®<p> 






'%' 






Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



518 



>r *>i 



\ r ^pjJi 5jj-- 



"Mukudzipangira milungu ina 
kusiya lye, (Milungu) yomwe 
siingadzibweretsere Zabwino 
kapena kudzichotsera sautso?" 
Nena: "Kodi angakhale ofanana 
wakhungu Ndi wopenya? Kodi 
kapena ungafanane Mdima ndi 
kuunika?" Kapena ampangira 
Anzake Mulungu omwe adalenga 
zofanana Ndi zomwe Mulungu 
adalenga kotero kuti Zolengedwa 
(zambali ziwirizo) zikufanana Kwa 
iwo? Nena: "Mulungu ndiye 
Mlengi wa Chilichonse. Ndipo lye 
ndi Mmodzi Wayekha, 
Wopambana (ndipo chimene lye 
wafuna Ndi chimene 
chimachitika") 

17. Adatsitsa madzi, kuchokera 
kumitambo, ndipo Zigwa 
zidayendetsa madzi mwa mlingo 
wake. Ndipo msefukiro 
wamadzi,udatenga thovu Lomwe 
limayandama pamwamba pamadzi. 
Ndiponso zomwe amazisungunula 
Pamoto chifukwa chofuna 
zodzikongoletsera Nazo kapena 
ziwiya (monga zagolide ndi 
Siliva), mukhalanso thovu 
chimodzimodzi. Umo ndi mom we 
Mulungu akuperekera Fanizo 
lachoonadi ndi fanizo lachonama. 
Tsono thovu, limangopita monga 
zitakataka Chabe; koma zimene 
zimathandiza anthu, 









Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



519 



\T %$r\ 



> T JLP^il «jj-» 



Zimakhazikika m'nthaka. Umo ndi 
m'mene Mulungu akuperekera 
Mafanizo. 1 

18. Amene adavomera Mbuye 
wawo, adzapeza Zabwino. Koma 
amene sadamuvomere, ngakhale 
Akadakhala nazo zonse zam'dziko 
ndi zina Zonga izo pamodzi, 
ndikuzipereka kuti Adziombolere 
(sizikadavomerezedwa). Ndipo 
Iwo adzakhala ndi chiwerengero 
choipa. Ndipo malo awo ndi ku 
Jahannama, (Amenewo) ndi malo 
oipakwabasi! 

19. Kodi amene akudziwa kuti 
Zimene zavumbulutsidwa Kwa 
iwe kuchokera kwa Mbuye wako 
nzoona, Angafanane ndi yemwe ali 
wakhungu? Ndithudi eni nzeru ndi 
okhawo olingalira; 

20. (Iwowo ndi) omwe 
akukwaniritsa lonjezo La 
Mulungu, ndipo saswa lonjezo 
lomangika (Pakati pawo ndi 
anzawo); 

21. Ndiponso omwe 
akulumikiza zomwe Mulungu 
Walamula kuti zilumikizidwe 
(monga chibale) Pamodzi ndi 
kuopa Mbuye wawo ndi kuopanso 















1 Nthawi zambiri zinthu zachabe zimagundika kwambiri, koma sizikhalira 
kuzimilira. Choncho.nkofunika kwa anthu kuchenjera ndi zinthu zotere. 
Asazikhulupirire chifukwa choona kuti zagundika, koma azipenyetsetse bwino, 
mofatsa kuti kuona kwake kwa zinthu kutsimikizike kwa iye. 



Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



520 



)T *>i 



^ t j&J\ 3jj-*» 



Chiwerengero choipa (chomwe 
chidzawapeza Oipa tsiku 
lachimaliziro tero amayesetsa 
Kuwapatuka machitidwe oipa); 

22. Ndi omwenso amapirira 
Chifukwa chofuna chiyanjo cha 
Mbuye wawo Ndi kupemphera 
Swala ndi kupereka zomwe 
Tawapatsa, mobisa ndi moonekera, 
Ndi kuchotsa choipa ndi chabwino 
(Pochita chabwino pachoipacho); 
iwo Ndi omwe adzapeza malipiro 
(abwino) a kunyumba Ya tsiku la 
chimaliziro. 1 

23. Minda yamuyaya adzailowa 
Iwo (pamodzi) ndi amene adachita 
Zabwino mwa makolo awo, Akazi 
awo ndi ana awo; ndipo angelo 
Azikalowa kwa iwo khomo lililonse. 

24. (Uku akunena) "Salaamu 
Alayikamu (Mtendere Uli painu) 
chifukwa chakupirira kwanu 
(Pochita zabwino ndi kusiya zoipa 
ndi kukhala Mwaubwino ndi 
anzanu)! Taona kukhala bwino 
Zotsatira za nyumba ya tsiku la 
chimaliziro." 









Kunena kotj "Kupereka mobisa ndi moonekera", kukusonyeza kuti sadaka 
zomwe munthu akupereka asazifunire nthawi yake yeniyeni yoperekera. 
Koma nthawi iliyonse. Ngati nkofunika kupereka mobisa kuopera kuti omwe 
akupatsidwawo asanyozeke kumaso kwa anthu, apereke mobisa. Ndipo ngati 
nkofunika kupereka moonetsera, ncholinga choti anthu ena atsanzire, monga 
kusonkhetsa kwa poyera apereke moonekera. Tsono kunena kwakuti "kuchotsa 
choipa ndi chabwino," kukutanthauza kuti anthu amenewa akawachitira zoipa 
ena, iwo sabwezera zoipazo. Koma amapitiriza kuchitira anthu oipawo zabwino. 



Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 I 521 I > r *>» 



> T Js-J\ bjj-- 



25. Koma amene akuswa 
lonjezo la Mulungu (Ndi 
malonjezo a anthu anzawo) 
pambuyo Polimanga motsimikiza, 
ndi kumadula Chimene Mulungu 
walamula kuti Chilumikizidwe, ndi 
kumaononga padziko, Iwowo 

ndi wo adzapeza Temberero; 
ndiponso adzapeza nyumba yoipa. 

26. Mulungu amamtambasulira 
riziki amene Wamfuna, ndipo 
amamfumbatiranso 
(Kumchepetsera amene wamfuna). 
Ndipo Akusangalalira moyo 
wapadziko lapansi, Suli kanthu 
moyo wapadziko poyerekeza Ndi 
moyo wa Pambuyo pa imfa, koma 
ndi Chisangalalo chochepa basi. 

27. Ndipo amene 
sadakhulupirire akunena: "Bwanji 
Sizidatsitsidwe kwa iye zozizwitsa 
kuchokera Kwa Mbuye wake?" 
Nena: "Ndithu, Mulungu 
amalekerera kusokera amene 
Wamfuna (chifukwa chosafuna 
kutembenukira Kwa Iye 
Mulungu); ndipo amamuongolera 
Amene akutembenukira kwa Iye." 

28. "(Awa ndi) amene 
akhulupirira, ndipo Mitima yawo 
ikukhazikika pokumbukira 
Mulungu. Dziwani, pokumbukira 
Mulungu mitima imakhazikika 
(Imatonthola)" 









Kit "k ."ii ^i \~*a*<> ' w 






Siirat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



522 hr*j*-i 



\ T J*J\ Ojj-*» 



29. "Amene akhulupilira Ndi 
kumachita Zabwino, chisangalalo 
Nchawo ndi Mabwerero abwino." 

30. Momwemo takutuma kwa 
anthu omwe adapita Patsogolo 
pawo anthu ena (ndipo amva 
Nkhani zawo zonse); kuti 
uwawerengere Zimene 
tikukuvumbulutsira; koma iwo 
Akumkana (Mulungu) Wachifundo 
chambiri. Nena: "Iyeyo ndi Mbuye 
wanga! Palibe Wopembedzedwa 
mwachoonadi koma lye; 
Ndatsamira kwa lye, ndipo 
kobwerera kwanga Nkwa lye basi." 

31. Ndipo ikadakhalapo Qur'an 
yomwe chifukwa Chaiyo mapiri 
akadayendetsedwa (panthawi 
Yoiwerenga), kapena chifukwa cha 
iyo, Nthaka ikadang'ambidwa, 
kapena chifukwa Cha iyo, akufa 
akadalankhulitsidwa,(yochititsa 
Zimenezi ikadakhala Qur'an iyi. 
Koma ntchito ya Qur'an 
siimeneyo)! Zinthu zonse nza 
Mulungu. Kodi sadadziwebe 
amene Akhulupirira, kuti Mulungu 
akadafuna Akadawaongolera anthu 
onse (ku chisilamu; Akadawalenga 
monga Angelo opanda zilakolako 
Koma wawapatsa nzeru ndi 
zilakolako kuti Alimbane ndi 
ziwiri; ena apambane Ndikulowa 
kumunda wamtendere). Ndipo 
Tsoka silisiya kuwapeza amene 









Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 523 > ? *>» 



> T J*J\ ijf 



sadakhulupirire Chifukwa cha 
zomwe achita, kapena Litsika 
pafupi ndi dziko lawo kufikira 
Lonjezo la Mulungu lifike 
(lowachotsa Moyo), ndithudi, 
Mulungu saswa malonjezo (Ake). 

32. Ndipo ndithu adachitidwa 
chipongwe Aneneri Akale iwe 
usanadze koma ndidawalekerera 
amene Sadakhulupirire 
(sindidawalange mwachangu), 
Ndipo kenako ndidawathira 
dzanja. Kodi Chilango changa 
chidali chotani! 

33. Kodi amene akuimirira 
mzimu uliwonse Pazimene 
udapeza (kuti adzaulipire, Sindiye 
woyenera kupembedzedwa)? 
Ndipo Ampangira Mulungu 
anzake . Nena: "Atchuleni 
(Anzakewo)." Kodi kapena 
mukumuuza Zomwe sakuzidziwa 
pa dziko, kapena ndi Mawu chabe 
(opanda cholinga chilichonse 
Zomwe mukunenazo)? Koma 
amene sadakhulupirire 
akometsedwa ndi bodza lawoli 
Lamkunkhuniza, ndipo 
atsekerezedwa kunjira 
(Yachoonadi). Ndipo amene 
Mulungu wamulekerera Kusokera 
alibe muongoli (wina 
Wakumuongolera). 

34. Ali nacho chilango m'moyo 
wadziko lapansi, Koma chilango 









&&^ij$d&&% 



Siirat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



524 



>r tj±\ 



\ r j*J\ 5jj-- 



chapambuyo pa imfa nchokhwima 
Zedi; ndipo sadzakhala ndi mtetezi 
kwa Mulungu. 

35. Fanizo la Munda wa 
Mtendere umene Alonjezedwa 
amene akuopa Mulungu (uli Tere:) 
Pansi ndi patsogolo pake Ikuyenda 
mitsinje. Zipatso zake ndi Mthunzi 
wake nzanthawi zonse. Awa 
Ndiwo malekezero a omwe akuopa 
Mulungu; Koma malekezero a 
osakhulupirira ndi Kumoto basi. 

36. Ndipo (ena mwa) omwe 
tidawapatsa mabuku (Ayuda ndi 
Akhrisitu), akusangalalira Zimene 
zavumbulutsidwa kwa iwe (ndipo 
Akulowa m'Chisilamu). Koma ena 
mu unyinji Wa osakhulupirira 
akukana gawo lina la Nkhaniyi. 
Nena: "Ndalamulidwa 
kupembedza Mulungu basi; ndi 
kusamphatikiza (ndi China). 
Ndikuitanira kwa Iye,ndipo kwa 
lye ndiwo mabwerero anga." 

37. Ndipo momwemo 
taivumbulutsa (Iyi Qur'an) 
m'Chiarabu Kuti ikhale chilamulo 
(cha Mulungu). Ngati utsata 
zofuna zawo pambuyo Pokufika 
kuzindikiraku,sudzakhala ndi 
bwenzi Ngakhale mtetezi kwa 
Mulungu. 

38. Ndipo ndithu, tidatuma 
atumiki, patsogolo pako Iwe 
usanadze ndipo tidawalola kukhala 












\ 9 C 9 m £\ J *\*1**K **""{ * 






Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 



525 



>r t&\ 



\ T op^Ji 5jj-- 



Ndi akazi ndi ana; (sichachilendo 
iwe Kukhala ndi akazi ndi ana). 
Ndipo Nkosatheka kwa Mtumiki 
kudzetsa chozizwitsa Koma 
pokhapokha ndi chilolezo cha 
Mulungu. Nyengo iliyonse ili ndi 
lamulo lake Limene Mulungu 
adalilemba. (Nyengoyo Ikakwana, 
lamulo limadza). 

39. Mulungu amafafaniza 
zimene wafuna ndi Kulimbikitsa 
(kuti zisachoke zomwe wafuna), 
Ndipo gwero la malamulo onse lili 
kwa Iye(Mulungu). 

40. Ndipo ngati tikusonyeza 
zina mwa (zilango) Zimene 
tawalonjeza, kapena kukupatsa 
Imfa (usanazione zilangozo, 
ndithu, Ziwafikabe).Ndithu udindo 
wako ndi kufikitsa Uthenga basi 
(umene walamulidwa kuufikitsa 
Kwa iwo). Ife udindo wathu ndi 
kuwerengera (Zochita zawo). 

41. Kodi sadaone kuti 
tikulidzera dziko lawo Ndi 
kulichepetserachepetsera malire 
ake? Ndipo Mulungu amalamula 
(mwachilungamo) Palibe wotsutsa 
lamulo Lake. Ndipo lye 
Ngwachangu pakuwerengera. 

42. Koma amene adalipo kale 
iwo kulibe, Adachita ziwembu; 
koma kuononga Ziwembu zonsezo 
nkwa Mulungu basi. (lye) 


















Surat 13. Ar-Ra'd Juzu 13 526 * T *&\ 



^ t js-J\ ijj~> 



akudziwa zimene cholengedwa 
Chilichonse chachita. Ndipo 
osakhulupirira Adzadziwa zotsatira 
zabwino za Nyumba ya tsiku la 
chimaliziro kuti Zidzakhala zayani. 

43. Ndipo amene 
sadakhulupirire akuti iwe Sindiwe 
mtumiki. Nena: "Mulungu 
Akukwanira kukhala mboni pakati 
panga Ndi pakati panu (kuti ine 
ndine Mtumiki), ndiponso aja 
omwe ali ndi Nzeru ya m'Buku." 
(Monga ena mwa Ayuda ndi 
Akhrisitu omwe Adalowa 
Chisilamu). 



ejM&$to$£Z 







Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



527 



ST *>i 



^ i *-a^S «jj-» 



Siirat Ibrahim XIV 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Alif-Ldm-Ra. (Hindi) Buku 
lomwe talivumbulutsa Kwa iwe 
kuti uwatulutse anthu mumdima 
Ndikuwaika mkuunika - 
mwalamulo la Mbuye wawo - 
uwapititse kunjira ya Mwini 
Mphamvu zoposa, Woyamikidwa. 

2. Mulungu, Yemwe ndi Zake 
zonse zakumwamba Ndi pansi. 
Ndipo kuonongeka ndi Chilango 
chokhwima kudzatsimikizika Pa 
osakhulupirira. 

3. Amene akukondetsa moyo 
wadziko lapansi Kuposa moyo wa 
pambuyo pa imfa, ndipo 
Amatsekereza (anthu) kunjira ya 
Mulungu ndikufuna kuikhotetsa 
(pom we Njirayo njosakhota). Iwo 
ali Mkusokera kotalikana 
kwambiri (ndi Choonadi). 

4. Ndipo sitidamtume Mtumiki 
aliyense Koma ndi chiyankhulo 
cha anthu ake Kuti awafotokozere. 
Kenako Mulungu Akumsiya 
kusokera amene wamufuna 
(Chifukwa mwiniwake safuna 
kuongoka). Ndipo amamuongolera 
yemwe wamfuna, Ndipo lye 
Ngwamphamvu zoposa, 
Ngwanzeru zakuya. 






Q^j)!<ijU#l«ti>L. 



**ub 












' »-"»^<fi^ , '' 'ii£i .'*!?£» '""'i 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



528 



>r *>i 



S i f*-Aly! ^j-*» 



5. Ndipo ndithu tidamtumiza 
Musa ndi zozizwitsa Zathu 
(tidamuuza):"Achotse anthu Ako 
mumdima (waumbuli) ndi kuwaika 
Mkuunika (kwa chikhulupiriro) 
ndipo Uwakumbutse masiku a 
Mulungu (a masautso)". Ndithu, 
m'zimenezo muli zizindikiro kwa 
Yense wopirira, wothokoza. 

6. Ndipo (akumbutse anthu ako) 
pamene Musa Adauza anthu ake: " 
Kumbukirani mtendere Wa 
Mulungu umene uli painu pamene 
Adakupulumutsani kwa anthu a 
Farawo, Omwe adakuzunzani ndi 
chilango choipa. Ankazinga 
(kupha) ana anu aamuna ndi 
Kuwasiya amoyo ana anu aakazi; 
ndithu, M'zimenezi mudali 
mayeso aakulu ochokera Kwa 
Mbuye wanu." 

7. Ndipo ( kumbukani) pamene 
Mbuye wanu adalengeza kuti: 
"Ngati muthokoza, 
ndikuonjezerani; Ndipo ngati 
simuthokoza (Dziwani kuti) 
chilango Changa nchaukali." 

8. Ndipo Musa adati (kwa anthu 
ake): "Ngati inu mukana(pakusiya 
kuthokoza) Pamodzi ndi onse 
am'dziko, (Mulungu salabadira 
chilichonse Pazimenezo), ndithudi 
Mulungu Ngwachikwanekwane; 
Ngotamandidwa. 






A 















Siirat 14. Ibrahim Juzu 13 | 529 \>T *>i S i ^\y\ *jy 



9. Kodi siidakudzereni nkhani 
ya omwe Adalipo patsogolo panu? 
Anthu a Nuhi, Adi ndi Samud? 
Ndi omwe adadza Pambuyo pawo? 
Omwe palibe akuwadziwa 
Kupatula Mulungu. Atumiki awo 
adawadzera Ndi maumboni 
oonekera. Koma adabwezera 
Manja awo kukamwa kwawo 
(kusonyeza Kutsutsa), ndipo adati: 
"Ndithu, ife Tikuzikana zimene 
Mwatumizidwa nazo, ndipo Ife tili 
m'chikaiko pazimene mukuitanira. 
Ndiponso mchipeneko." 

10. Aneneri awo adati: "Kodi 
mwa Mulungu, Mlengi wa thambo 
ndi nthaka muli chikaiko? lye 
akukuitanani kuti akukhululukireni 
Machimo ami, ndikuti 
(mukakhulupirira) Akupatseni 
nthawi (pokutalikitsirani Moyo 
wanu) kufikira panthawi 
yoyikidwa." Adati: "Inu sikanthu 
kena koma ndinu anthu Ngati ife. 
Mungofuna kutitsekereza 
Kuzimene ankazipembedza 
makolo athu; Choncho 
tibweretsereni umboni woonekera." 

11. Aneneri awo adati kwa iwo: 
"(Zoonadi), Ife ndife anthu ngati 
inu,koma Mulungu Amamchitira 
zabwino yemwe wamfuna Mwa 
akapolo Ake. Ndipo ife tilibe 
Nyonga zokubweretserani 
chisonyezo Koma mwachilolezo 






«W*3fe 



V 









Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



530 



>r ^ 



\ i A-AljJJ 0jJ~* 



cha Mulungu. Ndipo Kwa Mulungu 
yekha atsamire Asilamu onse." 

12. "Nanga kwa ife kuli chiyani 
kuti Tisatsamire kwa Mulungu 
Pomwe watisonyeza Njira zathu. 
Ndipo tipirira pa Zimene 
mukutisautsa nazo. Choncho, kwa 
Mulungu yekha atsamire otsamira." 

13. Ndipo amene 
sadakhulupirire, adanena Kwa 
Atumiki awo: "Ndithu, 
tikukutulutsani M'dziko lathu, 
pokhapokha mubwerere 
M'chipembedzo chathu." Koma 
Mbuye wawo (Mulungu) 
adawavumbulutsira uthenga 
(Wakuti): "Ndithu, tiwaononga 
Ochita zoipa (osakhulupirira)". 

14. "Ndipo tikukhazikani (inu) 
Pambuyo pawo m'dzikomo. Apeza 
zimenezi omwe aopa Kuimirira 
pamaso pa Ine, ndi kuopa 
Machenjezo Anga." 

15. Ndipo (aneneriwo) 
adapempha chithandizo (Kwa 
Mulungu), ndipo adaonongeka 
Aliyense wodzikuza, wamakani. 

16. (Yemwe) kutsogolo kwake 
Jahannama ikumdikira, ndipo 
(kumeneko) Adzamumwetsa 
madzi amafinya (otuluka 
M'matupi a anthu a kumoto). 

17. Adzakhala akumwa Koma 
movutikira Ndipo ululu wa imfa 












^m^o^m 



4& 



°v:^ 



«S^£5%JS%&gK 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



531 



>r ijk\ 



^ t psA\y.\ «jj-> 



Udzamdzera mbali zonse koma 
Sadzafa; ndipo kuonjezera apo, 
Pali chilango (china) chaukali. 

18. Fanizo la amene 
sadakhulupirire Mbuye Wawo, 
zochita zawo (zabwino zomwe 
Sadzalipidwa nazo chabwino 
chilichonse Chifukwa chakuti 
sadazichite pofuna Kukondweretsa 
Mulungu) zili ngati phulusa lomwe 
likuulutsidwa ndi mphepo ya 
mkuntho: ndipo sadzatha 
kupindula chilichonse pa zimene 
adachita, uko ndikutaika konka 
nako kutali (ndi choonadi). 

19. Kodi siuona kuti Mulungu 
adalenga thambo Ndi nthaka 
mwachoonadi? Ndipo atafuna 
Angakuchotseni (nthawi imodzi) 
ndikubweretsa Zolengedwa zina 
zatsopano. 

20. Ndipo zimenezo kwa 
Mulungu sizovuta. 

21. Ndipo onse (adzatuluka 
m'manda mwawo ndiponso) 
Adzakaonekera kwa Mulungu 
(kuti awalipire). Pamenepo ofooka 
(omwe adasokera chifukwa 
Chotsatira atsogoleri awo) 
adzanena kwa Omwe ankadzikuza: 
"Ndithu, ife tidali Kukutsatirani 
inu; kodi inu simungathe 
Kutichotsera kachinthu kochepa 
m' chilango Cha Mulunguchi?" 









&O0 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



532 ir*>i 



1 t ^1^1 OjJ-M 



(Atsogoleri) adzati: "Mulungu 
akadationgolera, 
tikadakuongolerani; (Koma 
tsopano) ndi chimodzimodzi kwa 
ife Titekeseke ndi chilangochi, 
kapena tipirire Nacho; tilibe 
pothawira." 

22. Ndipo Satana adzanena 
chiweruzo chikadzalamulidwa (Oipa 
kulowa kumoto, abwino Kulowa 
kumunda wamtendere): "Ndithu 
Mulungu Adakulonjezani lonjezo 
loona (ndipo Wakwaniritsa). Nane 
ndidakulonjezani, Koma 
sindidakukwaniritsireni. Ndidalibe 
Mphamvu pa inu 
(yokukakamizirani kunditsata) 
Koma ndimangokuitanani basi, 
ndipo Munkandiyankha. Choncho 
musandidzudzule, Koma 
dzidzudzuleni nokha. Sindingathe 
Kukuthangatani ndiponso inu 
simungathe Kundithangata. Ndithu, 
ine ndidakukana Kundiphatikiza 
kwanu ndi Mulungu kale. Ndithu, 
ochita zoipa adzapeza chilango 
Chowawa." 

23. Ndipo amene adakhulupirira 
ndikuchita zabwino, 






<*^^\p\&$&% 



Omasulira Qur'an adati: Chiweruzo chikadzaweruzidwa, anthu abwino 
nkukakhazikika kumunda wamtendere pomwe anthu oipa kukalowa kumoto, 
anthu akumoto adzayamba kumadzudzula Satana ndi kumnyoza. Ndipo 
Satana adzaimirira pakati pawo pagome lamoto m'katikati mwa Jahannama 
nadzanena kwa anthu onse akumoto kuti: "Musandidzudzule, koma dzudzulani 
mitima yanu. Mitima yanu ndiyomwe idakuonongani. Ine ndinkangokuitanani 
chabe, sindidakukakamizeni". 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



533 h^>> 



\ t +~*\jl\ *JJ~>> 



Adzalowetsedwa kuminda yomwe 
pansi Ndi patsogolo pake mitsinje 
ikuyenda, Adzakhala m'menemo 
muyaya mwachilolezo cha Mbuye 
wawo. Kulonjerana kwawo 
m'menemo Kudzakhala: 
"Mtendere! " 

24. Kodi suona momwe 
Mulungu waponyera Fanizo la 
liwu labwino? Liwu labwino Lili 
ngati mtengo wabwino (umene) 
mizu Yake njolimba, ndipo 
nthambi zake zanka Kumwamba, 

25. Umapereka zipatso zake 
nthawi iliyonse Mwachifuniro cha 
Mbuye wake. (Umo ndi momwe 
Liwu labwino lilili, limabwera ndi 
Zabwino). Ndipo Mulungu 
amaponyera anthu Mafanizo kuti 
akumbukire. 

26. Tsono fanizo la liwu loipa, 
lili ngati Mtengo woipa, umene 
Wazulidwa m'nthaka omwe Uli 
osalimba. 

27. Mulungu amawalimbikitsa 
amene Akhulupirira ndi mawu 
olimba m'moyo Wadziko lapansi, 
ndi moyo wapambuyo Pa imfa; 
ndipo Mulungu amawalekerera 
kusokera Omwe akudzichitira 
okha zoipa; ndipo Mulungu 
amachita zimene wafuna. 

28. Kodi sudawaone omwe 
asintha mtendere wa Mulungu 












W#fZ2$$&$$&$ 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



534 



S T *j£-l S t p-»\j>l 5j>-» 



moukana ndikuwafikitsa anthu 
awo (Omwe adawatsata m'zoipa) 
kunyumba ya Chionongeko? 

29. (Yomwe ndi) Jahannama; 
Adzailowa; taonani Kuipa malo 
okhazikikapo! 

30. Ndipo ampangira Mulungu 
anzake kuti Asokeretse (anthu) 
kunjira Yake! Nena: "Sangalalani 
pang'ono chabe! Ndithu, 
kobwerera kwanu nkumoto!" 

31. Auze akapolo Anga amene 
akhulupirira Kuti apemphere swala 
ndikupereka zina Mwazomwe 
tawapatsa, mobisa ndi moonekera 
Lisanawafike tsiku lopanda 
(chithandizo Cha) kudziombola 
ndi (chithandizo Cha) ubwenzi. 

32. Mulungu ndiYemwe 
adalenga thambo ndi Nthaka, 
ndipo adatsitsa madzi ku mitambo, 
Ndi madziwo adatulutsa zipatso 
kuti zikhale Riziki lanu (chakudya 
chanu) Ndipo adakufewetserani 
zombo Kuti ziziyenda panyanja 
mwa Lamulo Lake; ndiponso 
adakufewetserani Mitsinje. 

33. Adakufewetseraninso 
dzuwa ndi Mwezi, mopitirira 
(nthawi zonse) Ndiponso 
adakufewetserani Usiku ndi usana. 

34. Ndipo wakuninkhani 
zimene mwampempha (Ndi 
zimene simudam'pemphe). Ngati 



®&M&&P$ 









U&Z&xS&fSZ 









Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



535 



\T tj*r\ 



> i *-Ai^S *jj** 



Mutayesa kuwerenga madalitso a 
Mulungu, simungathe 
kuwawerenga. Ndithu, munthu 
ngwachinyengo Chachikulu 
ngosathokoza. 

35. Ndipo (kumbukani) pamene 
Ibrahim adanena: "Mbuye wanga! 
Uchiteni mzinda uwu (Wa Makka) 
kukhala wamtendere; Ndipo 
ndipatuleni ine ndi ana anga 
Kumachitidwe opembedza 
mafano." 

36. "Mbuye wanga! Ndithu, 
(mafano) Awa asokeretsa anthu 
ambiri. Choncho Amene 
wanditsata, ndithu iyeyo ali mwa 
ine (Mudzamulipira chabwino 
monga Mwandilonjeza), ndipo 
amene wandinyoza, (Mutha 
kumukhululukira) ndithu Inu 
Ngokhululuka kwambiri 
Ngwachisoni." 

37. "Mbuye wanga! Ndithu ine 
ndaikhazika Ina mwa mbumba 
yanga (mwana wanga Ismail) 
pachigwa ichi (cha Makka) 
Chopanda zomera panyumba yanu 
Yopatulika (Al-ka'ba); Mbuye 
Wathu (aloleni) kuti akhale 
opemphera Swala; Choncho 
ichiteni mitima ya anthu kukhala 
Yopendekera kwa iwo (akonde 
kudzakhala Malo amenewo), ndipo 
apatseni Zipatso kuti athokoze." 



ft&4& 












* 9&S9*' 9}<"< 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



536 



>r *jJh 



) t +*A\ji\ «JJ~»» 



38. "Mbuye wathu! Ndithu Inu 
mukudziwa Zimene tikubisa ndi 
zomwe tikuonetsa Poyera. Ndipo 
palibe chilichonse Chobisika kwa 
Mulungu, m'dziko kapena 
Kumwamba. 

39. "Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu Yemwe Wandipatsa ine 
kuukulu Ismail ndi Isihaka. 
Ndithu,Mbuye wanga Ngwakumva 
Pempho (la kapolo Wake)." 

40. "Mbuye wanga! Ndichiteni 
kukhala Wopemphera swala 
pamodzi ndi mbumba Yanga. 
Mbuye wathu! Landirani 
Zopempha zanga." 

41. "Mbuye wathu! 
Ndikhululukireni ine Ndi makolo 
anga ndi amene akhulupirira, 
(Makamaka) patsiku la 
chiwerengero (Kiyama)!. 

42. Ndipo usaganize kuti 
Mulungu waiwala zomwe 
Akuchita oipa. Ndithudijye 
akuwalekerera Chabe mpaka tsiku 
lomwe Maso awo adzatong'oke 
(Chifukwa cha mantha), 1 

43. (Adzakhala) akuyenda 
mothamanga mitu ili M'mwamba 
ndipo maso awo osatha kuphethira, 



tertL* ir^J Irtrff* {&** lOj 






1 Ndithudi machitidwe a Mulungu nkuwalekerera oipa pamene akuchita zoipa. 
Sawalanga mwachangu. Koma akafuna kuwalanga amawakhaulitsa ndi 
chilango choopsa. Choncho munthu asanyengedwe pamene akulakwira 
Mulungu namulekerera osamulanga. 



Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



537 



ir *>i 



\ t f-A'y! 5jj-*» 



Ndipo m'mitima mwawo muli 
mopanda kanthu (Mopanda ganizo 
lililonse chifukwa cha 
Kudzadzidwa ndi mantha). 

44. Ndipo achenjeze anthu za 
tsiku lomwe Chilango 
chidzawadzera; ndipo amene 
Ankadzichitira okha zoipa 
adzakhala akunena: "Mbuye 
wathu! Tichedwetseni kanthawi 
Kochepa (tipatseninso mwawi kuti 
tibwerere Pa dziko); tikayankhe 
kuitana kwanu ndi Kuwatsata 
Atumiki." (Adzauzidwa): "Kodi 
simunkalumbira kale kuti inu 
Simudzachoka (pa dziko)? 

45. "Chikhalirecho mudakhala 
m'malo mommuja Mwa omwe 
adadzichitira okha zoipa; ndipo 
Kudaonekeratu poyera kwa inu 
mmene tidawachitira 
(Powaononga); ndipo 
tidakufotokozerani Mafanizo 
(osiyanasiyana koma inu 
mudatsutsa)" 

46. Ndithudi, adachita ziwembu 
zawo, koma ziwembu Zawo zili 
kwa Mulungu (akuzidziwa 
bwinobwino); Ndipo ziwembu 
zawozo ngakhale zitatha 
Kuchotsetsa mapiri (sangamchite 
kanthu Mtumiki 

Muhammad {SAW} popeza 
Mulungu Wamteteza). 



^wjfejsayy^i 



% 



■si' 'Ai.'" »*y >\ \"\ 



titer 









Surat 14. Ibrahim Juzu 13 



538 



>r *>i 



) t f-*'^! «jj-*» 



47. Choncho usaganize kuti 
Mulungu Ngwakuswa Lonjezo 
Lake kwa Aneneri Ake. Ndithu, 
Mulungu ndi mwini Mphamvu 
(salephera Chilichonse), 
Ngobwezera chilango mwaukali. 

48. (Likumbukireni) tsiku 
lomwe nthaka iyi Idzasinthidwa 
kukhala nthaka ina (Yachilendo), 
ndi thambonso (lidzakhala Lina), 
ndipo iwo (anthu onse adzatuluka 
M'manda mwawo) adzaonekera 
pamaso pa Mulungu Mmodzi 
Wamphamvu (zopanda malire); 

49. Ndipo oipa udzawaona 
Tsiku limenelo Atanjatidwa ndi 
unyolo; 

50. Zovala zawo zidzakhala 
zaphula, ndipo Moto udzavindikira 
nkhope zawo; 

51. Kuti Mulungu aulipire 
mzimu uliwonse Pa zomwe 
udakolola; ndithu; Mulungu 
Ngwachangu pakuwerengera. 

52. Izi zikukwana kukhala 
phunziro kwa Anthu kuti 
achenjezedwe nazo, ndi kuti 
Azindikire kuti lye (Mulungu) ndi 
Mulungu Mmodzi basi, ndikuti eni 
nzeru akumbukire. 



&$w*&ypte&3& 



~ JM W'.Z 



&*#>£&' 









J&^ij&Jy^&Z&Z 



3?" 



&&^VuZ&&\6M 



VWit 



M3i 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



539 



>t t$r\ 



> j*t}~\ djj~> 





SURAT AL-HIJR XV 



Sura yolemekezeka ikulongosola zoyenera mwa zilango 
zomwe zidawatsikira anthu amibadwo yakale chifukwa 
chakunyoza kwao Atumiki a Mulungu. Ndipo ikufotokozanso 
nkhani za Aneneri akale ndi mavuto omwe adawapeza kwa 
anthu awo. Ndiponso ikusonyeza za Mulungu ndi za 
chilengedwe monga thambo lotukuka lokhala ndi nyenyezi ndi 
nthaka yoyalidwa bwino ngati mphasa momwe mkati mwake 
muli mapiri ataliatali olimbitsa nthaka. 

Surayi ikufotokozanso za mphepo yomwe imatenga madzi 
ndi kuwafalitsa panthaka; yomwenso imabereketsa mitengo. 
Ndipo surayi ikupitirira ndi kulongosolanso za nkhondo yomwe 
idalipo pakati pa Adam, Hawa ndi satana wopirikitsidwa 
kuchifundo cha Mulungu; nkhondo yomwe ikupitirirabe mpaka 
pa tsiku la chimaliziro. Ndipo nkhondoyi njomenyana pakati pa 
chabwino ndi choipa. Malekezero ake adzakhala oipa kukalowa 
kumoto, abwino kukalowa kumtendere. 




Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



540 



U *>i 



> o j3*J-l 5jj-> 



Surat Al-Hijr XV 



ms ; ,,m& 



:t 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Alif-Ldm-Rd. Izi ndi aya za 
M'Buku (lomwe lasonkhanitsa 
chilichonse Chofunika,) 
lowerengeka momveka bwino. 

2. Nthawi zambiri omwe 
sadakhulupirire (Pamene 
adzakhala mkati mwa moto) 
Adzalakalaka kuti akadakhala 
Asilamu (Pamoyo wapadziko 
lapansi). 

3. Asiye azidya (chakudya 
monga momwe Zidyera nyama) 
ndi kusangalala; ndipo 
Chiyembekezo chiziwatangwanitsa 
ndi Kuwanyenga; posachedwa 
adziwa (Kuti zimene 
amaziyembekezerazo Nzabodza). 

4. Ndipo sitidaononge mudzi 
uliwonse (M'midzi yochita zoipa) 
koma udali ndi Nthawi yake 
(youwonongera) yodziwika. 

5. Ndipo palibe mtundu wa 
anthu umene Ungaitsogolere 
nthawi yake (yofera) Kapena 
kuchedwa (itakwana kale). 

6. Ndipo (osakhulupirira) 
akunena (Mwachipongwe) "E, iwe 
amene Wavumbulutsiridwa ulaliki! 
Ndithudi ndiwe wamisala. 



ofa&\<£®\&\j 



-^ 









f v \f ' \ , ^" j i.^'\»V l A' ' 9 J 









^^MWKbK: 



^S&sa 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



541 



M t£-\ 



> j*i-l 3jj-» 






^7m5&t&\ 



'9*.y 



7. "Bwanji iwe osatibweretsera 
angelo (Kuti akuchitire umboni) 
ngati uli mmodzi Waonena 
zoona?" 

8. (Mulungu akuwauza) Ife 
sititsitsa angelo Koma pokhapokha 
(tikawatuma kukapereka Chilango 
kuonongeka kwa anthu) 
Kutatsimikizika (kuti 
adzawaononge); Ndipo pamenepo 
sangapatsidwe nthawi 

9. Ndithu, Ife ndife omwe 
Tavumbulutsa Qur'an, Ndipo 
ndithudi, tiisunga. 1 

10. Ndithudi tidatuma Atumiki 
patsogolo Pako m'magulu (A 
anthu) akale, oyamba. 

11. Ndipo sadali kuwadzera 
Mtumiki Aliyense, koma 
ankamchitira chipongwe. 

12. Momwemo tikuupititsa 
(mkhalidwe Wachipongwewu) 
m'mitima mwa oipa, 

13. Koma saikhulupirira 
Qur'aniyi chikhalirecho Mafanizo 
a anthu oyamba awadutsa (Ndipo 
aona momwe tidawaonongera). 



1 Omasulira Qur'an adati Mulungu Mwini wake adalonjeza udindo woisunga 
Qur'an ndi kuiteteza kuti anthu asathe kuikapo manja awo posintha 
ndondomeko ya mawu ake kapena matanthandauzo ake, poonjezerapo 
malembo ena kapena kuchepetsa monga momwe zidachitikira ndi mabuku 
ena omwe Mulungu adawasiira anthu kuti awasunge ndi kuwateteza. 
Qur'an yomwe tikuwerenga lero ndi yomweyo imene idalinso kuwerengedwa 
m'nthawi ya Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
Palibe mawu oonjeza kapena kuchotsa. 



©sis 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 542 U *>» 



S j9^\ Ojj^t 



14. Ndipo tikadawatsekulira 
(awa osakhulupirira) Khomo 
lakumwamba ndipo nkukhala 
Akukwera m'menemo (ndi kutsika 
monga Momwe amafunira kuti 
zimenezo zikhale Chozizwitsa cha 
Mtumiki) 

15. Akadati: "Ndithu, maso 
athu aledzera; (Iyayi) koma ndife 
anthu olodzedwa (Tikuona zomwe 
sindizo)." 1 

16. Ndithudi, kumwamba 
tidaikako "Buruji" (Momwe 
zikuyendamo nyenyezi) ndipo 
Tidakukongoletsa kwa okuwona. 

17. Ndipo tidakuteteza kwa 
satana aliyense Wopirikitsidwa 
(kumwambako akafuna 
Kukamvetsera zimene 
zikunenedwa kumeneko). 

18. Kupatula amene 
amamvetsera mobera; Ndipo 
pompo chinsakali chamoto 
Choonekera chimamtsata. 

19. Ndipo nthaka tidaiyala ndi 
kuikamo Mapiri ndipo tameretsa 
mmera wa Chinthu chilichonse 
M'menemo mwamlingo (Wake). 

20. Ndipo mmenemo 
takupangirani zinthu Zoyendetsa 






%&C&x$zMl$ 



fo'H&& 



r^JiV-SJi *W^ jyw^oSj 



®£& J=^ C^vJQ&p-ji 



o^K*i\s f^<3J^^y[ 









1 Mulungu akuti akadawatsekulira makomo akumwamba monga momwe 
adafunira nakwerako nkuona ufumu wa Mulungu ndi angelo ali yakaliyaklai, 
sakadakhulupirirabe chifukwa chakuuma kwa mitima yawo. Chimene 
akadanena nkuti mitu yazungulira. 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



543 



W *>i 



\ O j^J-l Ojj-* 



moyo (wanu zakudya Ndi 
zakumwa ndi zina zotere) 
ndiponso (Tidakupatsani ana ndi 
ziweto) zomwe inu Simungathe 
kuzidyetsa. (Ife ndife amene 
Tikuzikonzera chakudya chawo, 
osati inu). 

21. Ndipo palibe chinthu 
chilichonse Koma gwero lake 
likuchokera kwa Ife; Ndipo 
sitichitsitsa koma mwamlingo 
Wodziwika (osati 
mwachisawawa) . 

22. Ndipo timazitumiza mphepo 
zitasenza madzi Ndipo madziwo 
tikuwatsitsa kuchokera 
Kumitamboyo; kenako 
tikukumwetsani Madziwo 
(tikukumwetseraninso ziweto zanu, 
Mitengo yanu ndi zina), ndipo inu 
siamene Mukuwasunga (madziwo). 

23. Ndipo ndithudi, Ife ndife 
omwe timapereka Moyo, ndi 
kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi 
Amlowam'malo (a chinthu 
chilichonse Chimene chikusiidwa 
chopanda mwini). 

24. Ndipo tikuwadziwa mwa 
inu amene atsogola (Amene adafa 
kale), ndipo tikuwadziwanso 
Amene atsalira (ali ndi moyobe ndi 
amene Sanabadwe). 

25. Ndipo palibe chikaiko, 
Mbuye wako ndi Yemwe 















%?&&&&!?&$& 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 I 544 \ i *> 



> jP^\ 5jj-*» 



adzawasonkhanitsa (pambuyo pa 
imfa Kuti adzawaweruze). lye ndi 
Wanzeru Zakuya, Wodziwa 
chilichonse. 

26. Ndipo ndithu, tidamlenga 
munthu ndi dongo Louma lolira 
lochokera kumatope odera, 
Osinthika mtundu; 

27. Ndipo ziwanda tidazilenga 
kale ndi Moto wamphepo yotentha 
kwambiri. 

28. Ndipo (kumbuka) pamene 
Mbuye wako adauza Angelo 
(kuti): "Ndithu, Ine ndilenga 
munthu Ndi dongo louma lolira 
lochokera Kumatope odera 
osinthika mtundu; 

29. "Choncho ndikamkwaniritsa 
Ndikumuuzira mzimu 
Wolengedwa ndi Ine, 
muweramireni Momulemekeza". 

30. Choncho angelo onse 
Adamuweramira. 

31. Kupatula Iblis; adakana 
Kukhala mmodzi Mwa owerama. 

32. Mulungu adati: "E, Iwe 
Iblis! Chifukwa ninji sudakhale 
Pamodzi ndi owerama?" 

33. Adati: "Sindingamuweramire 
Munthu yemwe mwam'lenga ndi 
Dongo louma lolira lochokera 
Kumatope odera osinthika 
mtundu." 



kn 



®j&* 



c^&Ja &QCjq\ uixi. o2S 















Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



545 



> i ^jJt-1 > O yjJ-l Oj^ 



34. (Mulungu) adati: "Choncho 
choka m'menemo; Ndithu, iwe 
ndiwe wopirikitsidwa (ku 
Chifundo changa). 

35. "Ndipo ndithu, 
matemberero ali pa iwe Mpaka 
tsiku lamalipiro." 

36. (Iblis) adati: "Mbuye wanga 
choncho Ndipatseni nthawi mpaka 
tsiku limene Adzaukitsidwe kwa 
akufa." 

37. (Mulungu) adati: "Ndithu, 
iwe ndi mmodzi Mwa opatsidwa 
nthawi (danga), 

38. Kufikira tsiku la nthawi 
yodziwika (Ikadzafika nthawi 
imeneyo, udzafa)" 

39. (Satana) adati: "Mbuye 
wanga! Pakuti Mwanena kuti 
ndine wosokera, choncho 
Ndikawakometsera za m'dziko 
(Kufikira kuti akakulakwireni) 
Ndithu, ndikawasokeretsa onse, 

40. Kupatula akapolo Anu 
oyeretsedwa, Mwa iwo". 

41. (Mulungu) adati: Iyi 
ndinjira yoongoka Yobwerera kwa 
Ine (ndipo adzandidzera 
Akadzafuna). 

42. Ndithudi akapolo Anga pa 
iwo sudzakhala Ndi mphamvu 
kupatula okutsata (Mwachifuniro 
chawo) mwa opotoka." 












Surat 15. AI-Hijr Juzu 14 546 \ t *j*-» \ ysJ-\ i^ 



43. Ndithu, Jahannama Ndiwo 
malo awo Olonjezedwa kwa onse. 

44. Hi ndi makomo asanu ndi 
awiri; Ndipo khomo lililonse lili 
ndi Gawo logawidwa mwa iwo. 

45. Ndithudi oopa Mulungu 
adzakhala M'minda ndi akasupe 
(Omwe adzakhala Patsogolo 
pawo), 

46. (Ndipo tidzawauza) 
"Lowani M'menemo 
mwamtendere, Mosatekeseka." 

47. Ndipo tidzawachotsera 
mfundo Zachidani zomwe zidali 
m'mitima Mwawo; (adzakhala) 
mwachibale, (Mokondana,) 
atakhala pamipando Yachifumu 
atayang'anizana nkhope. 

48. Mmenemo masautso 
Sakawakhudza, Ndiponso 
sadzatulutsidwamo. 

49. Auze akapolo anga kuti 
Ndithu Ine ndine Wokhululuka 
kwambiri, Wachisoni. 

50. Ndipo ndithu, chilango 
Changa ndi chilango Chopweteka 
zedi. 

51. Ndipo auze nkhani ya 
alendo a (Mneneri) Ibrahim. 

52. Pamene adalowa kwa iye 
ndikunena: "Salamu (Mtendere! 
Iyenso adawayankha" "Mtendere 



®&^&&4Xfe$& 



Jfori 












^4VS#&i&<8S 






Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 I 547 \i *j*-i ) y^\ 5j^ 



ukhalenso pa inu. "Ndipo Pamene 
adaona kuti akana Chakudya) 
Adati: "Ndithu ife tikukuopani." 

53. (Iwo) adati: Usaope! Ife 
tikukuuza Nkhani zabwino za (kuti 
ubala) mwana Wanzeru 
kwambiri." 

54. (lye) adati:"Ha! 
Mukundiuza nkhani Iyi pomwe 
ukalamba wandifikira? Kodi 
Nkhani yabwinoyi mukundiuza 
m'njira Yotani?" 

55. (Iwo) adati: "Takuuza 
nkhani yabwinoyi Mwachoonadi; 
choncho, usakhale mwa Otaya 
mtima." 

56. (lye) adati: "(I ne sinditaya 
mtima Ndi chifundo cha 
Mulungu). Ndithu, Palibe angataye 
mtima ndi chifundo cha Mulungu, 
koma wosokera basi (yemwe 
Sazindikira ukulu wa Mulungu)." 

57. (lye) adati: "Nanga 
Cholinga chanu china Nchiyani, E, 
inu otumidwa?" 

58. (Iwo) adati: "Ife 
Tatumidwanso kwa Anthu aja oipa 
(kuti tikawaononge). 

59. "Kupatula omtsatira Luti, 
ndithu ife Tikawapulumutsa onse," 

60. "Koma mkazi wake (Wa 
Luti), tampimira Kukhala mmodzi 
wa otsalira pambuyo." 



&&&mx$$$i 









Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



548 



U t>i 



> o j*J-\ ijj*j 



61. Ndipo pamene atumikiwo 
adadzera Anthu a Luti (okhala ali 
ndi maonokedwe Aumunthu). 

62. (Luti) adati: "Ndithudi, inu 
ndi anthu Osadziwika 
(sitikudziwani)." 

63. (Iwo) adati: "Inde, ife 
takudzera ndi zomwe (Iwo) adali 
kuzikaikira, (zomwe ndi Chilango 
chawo)." 

64. "Ndipo tadza kwa iwe ndi 
(chinthu) Choonadicho, ndithu ife 
ndi oona (pazimene Tinenazi). 

65. "Choncho, choka ndi banja 
lako mkati Mwa usiku; ndipo iwe 
udziwatsata Pambuyo pawo; tsono 
aliyense wa inu Asayang'ane 
kumbuyo (akamva mkokomo 
Wachilango chochokera 
kumwamba, kuopa Kuti angafe), 
ndipo yendani (mwachangu) 
Kunka komwe mukulamulidwa. 

66. Ndipo tidamudziwitsa 
iyeyo(Luti) lamulo lathu lakuti 
ndithu phata lawo 
anthu(ochimwawo)lidzadulidwa 
kum'banda kucha . 

67. Ndipo adadza (kwa Luti) 
anthu a M'mudziwo akusangalala 
(poona kuti Kwadza alendo okongola 
kuti achite Nawo zadama). 1 



^fti&Jlfc® 



%gtt$%K 



9&SC^&Ci$&£$£ 






? 



K' 






®v&03£^i$$& 



1 Anthu a mumzindawo adadza kunyumba ya Luti akuthamanga mokondwa 
atamva kuti kwa Luti kwadza alendo achinyamata owoneka bwino zedi. 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



549 



^ t tji-i ^ o jp^\ Ojj~i 



68. (Mneneri Luti) adati: 
"Ndithu, awa Ndialendo anga; 
choncho musandichititse Manyazi 
(pochita nawo zadama)." 

69. "Muopeninso Mulungu, 
ndipo Musandichititse manyazi 
(pamaso pawo)," 

70. Iwo adati (kwa Mneneri 
Luti): "Kodi Sitidakuletse 
kulandira anthu (Achilendo)?" 

71. (lye) adati: "Awa (akazi 
onse ali ngati) Ana anga. Ngati inu 
ndinu ochita (chimene 
Chalamulidwa, akwatireni; 
Musachite Zauve ndi alendowa)". 

72. Ndikulumbira moyo wako, 
ndithu Iwo m'kuledzera kwawo 
(ndi zoipa) Akungoyumbayumba. 

73. Choncho mkuwe wa 
chilango udawagwira Pamene 
dzuwa linkatuluka, 

74. Ndipo (midziyo) 
tidaigadabula kumwamba Kukhala 
pansi, (pansi kukhala 
Kumwamba); ndipo 
tidawavumbwitsira Mvula 
yamiyala (yotentha) yamoto. 

75. Ndithudi, (m'nkhani iyi) 
muli Malingaliro (aakulu) kwa 
anthu olingalira Zinthu. 



K&mi&$si®3s 



%&%^J££ 



%&&&&&$% 



®^M&mw& 



%&&&&$&%& 



%&J&2&\&8& 






®&£M^£ttiM 



Adabwera ndi cholinga chodzachita nawo zadama poganiza kuti alendowo 
adali anthu monga iwo. 



Surat 15. AI-Hijr Juzu 14 



550 



i 1 *j*-i > o y^t Sjj-*. 



76. Ndipo (midzi) iyi (yomwe 
tidaiwononga Chotereyi), ili 
chikhalire m'njira Moyenda anthu 
(ndipo iwo akuona Zizindikiro 
zake) 

77. Ndithudi, mzimenezi muli 
phunziro (Lalikulu) kwa 
okhulupirira. 

78. Ndipo,ndithu, anthu a 
m'nkhalango (Anthu a Mneneri 
Shuaibu) Adali ochita zoipa 
kwabasi; 

79. Choncho, tidawalanga. 
Ndipo (maiko) Awiriwa ali m'njira 
zoonekera, (momwe Akuraishi 
amadutsa pa maulendo awo). 

80. Ndipo ndithu, okhala 
m'chigwa cha Hijr, Adatsutsa 
atumiki. 

81. Tidawapatsa Zisonyezo 
zathu, koma Sadazilabadire. 

82. Iwo adali kujoba nyumba 
m'mapiri Mwamtendere 
(ankaboola mapiri Kuwasandutsa 
nyumba zawo). 

83. Choncho, chiphokoso cha 
chilango Chidawapeza m'mawa. 

84. Sichidawathandize (chuma) 
chomwe Ankachipeza 
(ngakhalenso zimene Ankazichita). 

85. Sitidalenge thambo ndi 
nthaka ndi (Zonse) zapakati pake 



wjwras 



® 



&£&&?****''" lMf '- 



\x<y®\z<s&a$@&Z 



Surat 15. Al-Hijr Juzu 14 



551 



> t frj*-l ^ ygJ-\ Ojj-* 



koma (Kulimbikitsa) choonadi. 
Ndipo palibe chikaiko, Kiyama 
idza. Choncho Mkhululukire 
kukhululuka kwabwino, (Aliyense 
wokuchitira zoipa). 

86. Ndithudi, Mbuye wako, lye 
ndi Mlengi Wa zonse, Wodziwa 
kwambiri. 

87. Ndipo ndithu, takupatsa 
(Aya izi) zisanu ndi Ziwiri 
zomawerenga kawirikawiri, (Surat 
Fatiha), ndi Qur'an yolemekezeka. 

88. Usatong'olere maso ako 
(kuyang'ana) Zimene 
tawasangalatsa nazo 
Mitundumitundu ya mwa iwo 
(monga chuma Cha anthu 
osakhulupirira). 

Usawadandaulirenso iwo ndipo 
tsitsa phiko Lako kwa 
okhululupirira, (uwafungatire 
Monga nkhuku ichitira ndi ana ake). 

89. Ndipo nena: "Ndithu, ine 
ndine Mchenjezi woonekera, 
(sindibisa chilichonse Kuopera 
kuti chingakugwereni chilango 
Cha Mulungu.)" 

90. Monga momwe Tidatsitsira 
(chilango) Kwa amene adadzigawa 
m'magulu. 

91. Omwe aichita Qur'an 
Kukhala zigawozigawo; (Zina 
nkuzikhulupirira, Zina 
nkuzitsutsa). 






^£&U Ji,e£££ &oJ£$ 



*^2&0&& 






Surat 15. AI-Hijr Juzu 14 552 > i *>* 



\ j*J-\ djj^ 



92. (Mulungu akuzilumbirira 
kuti) pali Mbuye wako, 
tidzawafunsa onse (Tsiku la 
Kiyama), 

93. Pazimene ankachita 
(Padziko lapansi) 

94. Choncho, lengeza zimene 
ukulamulidwa, Ndipo uwapewe 
Amshirikina, (usaope Chilichonse 
kwa iwo). 

95. Ndithu, Ife tikukwanira 
kukuteteza Ku (zoipa za) 
achipongwe. 

96. Omwe akupanga milungu 
Ina ndi kuiphatikiza Ndi Mulungu, 
posachedwapa adziwa. 

97. Ndithu, Ife tikudziwa kuti 
chifuwa Chako chikubanika ndi 
Zimene akunenazo. 

98. (Koma pirira), lemekeza 
Mbuye wako Pamodzi ndi 
kumtamanda (ndi mbiri Zake 
Zabwino) ndipo khala mwa 
olambira (Mulungu.) 

99. Ndipo mpembedze Mbuye 
wako mpaka Chikufike 
chitsimikizo (imfa). 



&S9 *>< 9 9+f'*^ 'V*"< 






%^\&&<$&i 






®d^<eS^(l>^o^S 




Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



553 



\ i *jA-l \ 1 J>lJ| Sj^- 




SURAT AN-NAHL XVI 

v~ ~fc . i . 



Sura iyi idavumbulutsidwa ku Makka, kupatula aya zitatu 
zomalizira, zidavumbulutsidwa ku Madina. Kuchuluka kwa aya 
zake ndi 128. 

Surayi yayamba ndi kulimbikitsa lonjezo la Chauta 
lachilango cha opembedza mafano. Ndipo yafotokoza za 
mphamvu za Mulungu pokwaniritsa zimenezo, komanso umboni 
wosonyeza kukhoza kwake, ndi kulenga kwake kwa thambo ndi 
nthaka. 

Kenako surayi yafotokoza za chisomo cha Mulungu chomwe 
chili pa anthu onse; monga powalengera ngamira ndi 
kuwameretsera mbewu ndi zomwenso adawalengera m'nyanja; 
monga nsomba zomwe iwo amadya, ndi majuwere 
(zozikongoletsera nazo zamtengo wapatali monga ndolo makoza 
zibangili ndi zina). Ndipo kenako surayi yalozanso zomwe 
zingafunike pachisomo chimenechi, monga kuyamika Mulungu 
ndi kupembedza lye yekha. 

Yafotokozanso zakunyalanyaza kwa opembedza mafano, za 
umodzi wa Chauta ndi kuinamizira Qur'an pomati ndi nthano 
zopeka za anthu akale. Ndipo Mulungu waloza za chilango cha 
Amshirikina patsiku la Kiyama, ndi za mtendere wa 
okhulupirira. 

Mulungu msurayi wafotokozanso mwatsatanetsatane kuti 
opembedza mafano akutsutsa zouka ku imfa. 




Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



554 1 * *>' 



> "V >Ji 3 jj- 



Surat Al-Nahl XVI 



3 r 



«2 



Q^JJI^JJI^I^. 



v^hj 






'tUfcWfti 



M'dzina la Mulungu waC hi/undo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Lamulo la Mulungu 
lidzafika, (ndithu) Choncho, 
musalifulumizitse; (ndipo 
Khulupirirani kuti lye ndi 
Mulungu) Woyera; Wopatukana 
ndi mbiri zopunguka, Ndipo 
watukuka ku Zomwe 
akumphatikiza nazo. 

2. Amatumiza Angelo pansi 
pamodzi ndi Chivumbulutso mwa 
lamulo Lake (Mulungu), Kwa omwe 
wawafuna mwa akapolo Ake 
(Powauza) kuti achenjezeni (anthu 
zakuti) Palibe wopembedzedwa 
mwachoonadi koma Ine ndekha, 
choncho ndiopeni." 

3. Adalenga thambo ndi nthaka 
mwachoonadi (Osati 
mwakungoseweretsa chabe) ndipo 
Watukuka kuzimene 
akumphatikiza nazo (Ophatikiza 
Mulungu ndi mafano). 

4. Adalenga munthu kuchokera 
kudontho la Umuna; ha! kenaka iye 
(munthuyo) Wakhala wotsutsana 
naye (Mulungu) Woonekera. 1 

1 Apa Mulungu akunenetsa kuti adalenga munthu kuchokera kudontho la 
umuna wopanda pake. Koma munthu pambuyo pokwanira chilengedwe chake 
akukhala wotsutsana ndi Mlengi wake ndi kumchitira mwano modzitukumula 
chikhalirecho adalengedwa kuti akhale kapolo wa Mulungu, osati wopikisana naye. 






m?&&Qzi\&L 






Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



555 



U ^>> 



\ n j^ji *jj~< 



5. Ndipo adalenga ziweto 
(monga ngamira, Ng'ombe ndi 
mbuzi) mwa izo mukupeza 
Zofunda, ndi zothandiza (zina 
zambiri), Ndipo zina mwa izo 
mumazidya 

6. Ndipo mumakondwa ndi 
kunyadira chifukwa cha 
Kukongola kwa izo mukamabwera 
nazo (Kuchokera kubusa mimba 
zitakhuta), Ndi popita nazo 
(kumunda ndi kubusa Zikuyenda 
mwandawala). 

7. Ndipo zimasenza mitolo yanu 
(yolemera) kukafika Nayo kumidzi 
yakutali komwe simumatha 
Kukafikako popanda kuvutika 
kwambiri.Ndithu, Mbuye wanu 
Ngodekha kwabasi, Ngwachisoni. 

8. (Adalenganso) akavalo, 
nyumbu ndi abulu Kuti 
muzizikwera ndi kutinso zizikhala 
Chokometsera chanu (cholowetsa 
chisangalalo M'mitima yanu); 
ndipo adzalenga (zokwera Zina) 
zomwe simukuzidziwa, (monga 
galimoto, Sitima, ndege ndi zina). 

9. Ndipo ndi udindo wa 
Mulungu kusonyeza Njira 
yolungama (yomwe 
ingakufikitseni Kumunda 
wamtendere), koma zilipo njira 
Zina zokhota (zomwe sizifikitsa 
kuchoonadi). Ndipo Mulungu 
akadafuna, akadakuongolani 



&r-- •* 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



556 



>i »>l 



> ■; j>jt Sj^ 









®, 



Nonsenu (mwachifiiniro chanu ndi 
mopanda Chifuniro chanu.Koma 
lye adakupatsani nzeru Kuti 
musankhe nokha njira imene 
mufuna) 

10. lye ndi Amene 
akukutsitsirani madzi Kuchokera 
kumitambo, madziwo mumamwa 
(Pothetsa ludzu lanu), ndipo ndi 
madziwo Mitengo imamera; 
mitengo yomwe mumadyetsa 
Ziweto (zanu). 

11. Ndi madzi omwewo 
amakumeretserani mmera, 
(Mitengo ya) mzitona, kanjedza, 
mpesa, Ndi mitundu ina yonse 
yazipatso. Ndithu Kupezeka kwa 
zimenezi ndi chisonyezo 
(Chosonyeza mphamvu za 
Mulungu) kwa Anthu olingalira. 1 

12. Ndipo chifukwa cha inu 
adagonjetsa usiku Ndi usana; 
dzuwa ndi mwezi; (zonse 
Zidalengedwa kuti zibwere ndi 
zokomera inu). Nazo nyenyezi 
zidagonjetsedwa mwa lamulo 
Lake. Ndithu m'zimenezi muli 
zizindikiro Kwa anthu anzeru. 

13. Ndiponso ndi zimene 
adakulengerani m'nthaka (Zinthu 

1 Ndithudi, m'kutsika kwa madzi kuchokera kumitambo ndi ku me rets a zipatso, 
muli zisonyezo zoonekera poyera kukhoza kwa Mulungu ndi umodzi wake 
kwa anthu omwe amalingalira za zolengedwa Zake. Ndipo potero 
amakhulupirira Mulungu Kodi simukuona mbewu imodzi ikaikidwa m'nthaka 
ndi kupitapo nyengo yodziwika, imafunafuna potulukira ndi kung'amba nthaka 
ndi kukula kusanduka mtengo? Zonsezi nzododometsa kwa anthu olingalira. 



U 






^kj®dwB^ 



Sural 16. Al-Nahl Juzu 14 



557 hi »>i 



^ 1 >cJl J,^, 



^avsr^asf^a 



©,■'*' 



'(aa>»oJ 






©6$%2U& 



zododometsa monga nyama, 
mmera, Miyala yamtengo 
wapatali, zamoyo ndi Zopanda 
moyo), zautoto wosiyanasiyana ndi 
Maonekedwe osiyanasiyana; 
ndithu, M'zimenezo muli 
zisonyezo kwa anthu Olalikika. 

14. Ndipo lye ndi Yemwe 
adagonjetsa nyanja Kuti mudye 
nyama yamatumbi (ya) m'menemo 
(Nsomba) ndikuti mutulutse 
m'menemo Zodzikongoletsera 
zomwe mumavala; ndipo Uona 
zombo zikuluzikulu zikung'amba 
(Mafunde) m'menemo kuti 
mufunefune Zabwino zake (njira 
ya malonda), ndi kuti Muthokoze 
(Mbuye wanu Mulungu). 

15. Ndipo adaika panthaka 
mapiri ataliatali Kuti (nthaka) 
isagwedezeke nanu; ndipo 
(Adaika) mitsinje ndi misewu kuti 
muongoke (Potsata njira yeniyeni 
ndikukafika komwe Mukufuna). 1 

16. Ndipo (adaikanso) 
zizindikiro zina, Ndiponso 
kupyolera m'nyenyezi, iwo 
Amalondola njira. 

17. Kodi Yemwe amalenga 
angalingane ndi omwe Salenga? 

1 Mulungu adakhazikitsa mapiri ataliatali, olimba kuti nthaka isamagwedezeke 
pafupipafupi. Abu Suud adati: "Ndithudi nthaka idalengedwa ngati mpira 
ndikukhala yogwedezeka pazifukwa zochepa asanailengere mapiri monga 
momwe zimagwedezekera nyenyezi zinzake. koma pamene adailengera 
mapiri idakhazikika. Zoterezi ndi pachifukwa chakuti anthu akhazikike bwino. 



%:-"- ' 






®&&&J$&£& 



<%3$®8^ufi§*& 



Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 558 U *>i ^ n J~Ji3j>- 



Kodi simungakumbukire 
(Ndikudziwa kulakwa kwanu 
pomuyerekeza Mulungu ndi 
mafano)? 

18. Ngati mutayesera 
kuwerengera mtendere Wa 
Mulungu simungathe 
kuuwerengera (Wonse); ndithudi, 
Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri, Ngwachisoni. 

19. Ndipo Mulungu akuzidziwa 
Zimene mukuzibisa, Ndi zomwe 
mukuwonetsera. 

20. Ndipo zomwe 
mukuzipembedza kusiya Mulungu, 
sizilenga chilichonse, ndipo Izo 
nzolengedwa. 

21. Zakufa zopanda moyo; 
ndipo Sizizindikira kuti nliti akufa 
Adzaukitsidwa (m'manda 
mwawo). 

22. Mulungu wanu ndi 
Mulungu mmodzi Yekha; koma 
amene sakhulupirira Za tsiku la 
chimaliziro, mitima yawo Ikukana 
(kukhulupirira umodzi wa 
Mulungu), Ndipo iwo 
akudzitukumula. 

23. Palibe chikaiko, Mulungu 
akudziwa zomwe Akubisa, ndi 
zomwe akuzilengeza. Ndithudi, 
lye sakonda odzikuza. 

24. Ndipo (osakhulupirira) 
akafunsidwa: Kodi Mbuye wanu 






$' *99*~'X' '£X'9<V: 1$ i'*< 






Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



559 



U *jk-\ 



) "V J*cJl 5jj-» 



•* 






watumizanji (kwa Mneneri 
Muhammad{SAW})"? Akunena, 
(sadatumize Chilichonse koma) 
nthano zabodza za Anthu akale." 1 

25. (Motero akuwasokeretsa 
anthu) kuti Adzasenza mitolo 
yawo (yamachimo) Yokwanira pa 
tsiku la Kiyama, Ndiponso gawo 
lamitolo ya omwe Akuwasokeretsa 
popanda kuzindikira (Osokerawo). 
Tamverani! Ndi yoipa Kwabasi 
mitolo yomwe azikaisenza! 

26. Adachita ndale omwe 
adalipo Patsogolo pawo; choncho 
Mulungu Adagumula maziko 
anyumba zawo. Ndipo madenga 
adawagwera Pamwamba pawo; 
ndipo Chilango chidawadzera 
Kuchokera komwe sadali 
kukudziwa. 

27. Kenako tsiku la Kiyama 
adzawayalutsa Ndi kunena: "Ali 
kuti omwe mudali Kundiphatikiza 
nawo, omwe chifukwa cha Iwo 
mudali kukangana (ndi 
Mtumiki)?" Adzanena omwe 
apatsidwa nzeru: "Ndithu, 
Kuyaluka ndi tsoka loipa zili pa 
Osakhulupirira lero," 

28. Omwe angelo akutenga 
miyoyo yawo Atadzichitira okha 

1 Omasulira Qur'an akunena kuti, amshirikina adali m'njira zolowera mumzinda 
wa Makka ndi cholinga chopatula anthu kwa Mtumiki (SAW). Anthu odzachita 
haji akawafunsa kuti:"Kodi nchiyani chavumbulutsidwa kwa Muhammad?" Iwo 
amati: "Ndi nthano zabodza za anthu akale osati Mawu a Mulungu." 



^SJSii&Ugte 



2^ &&$£=£& 



mm\&z;&$\ 



Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 560 ^ t *>i 



1 1 J~Jl 5j>w 



zoipa (ponyoza Mulungu). 
Choncho adzadzipereka (kwa 
Angelowa, kuti atenge mitima 
yawo Akunena:) "Sitidali kuchita 
choipa Chilichonse." (Angelo 
adzati:) "Zoona, Palibe chikaiko, 
Mulungu akudziwa kwambiri 
Zomwe munkachita; 

29. Choncho, lowani makomo a 
ku Jahannama; Mukakhala 
m'menemo muyaya." Taonani 
Kuipitsitsa kwa malo a anthu 
odzikweza! 

30. Ndipo kukanenedwa kwa 
omwe akuopa Mulungu (kuti): 
"Kodi nchiyani watumiza Mbuye 
wanu?" Amati: "Zabwino." Kwa 
omwe achita zabwino padziko ili 
Lapansi, awapatsanso zabwino, 
ndipo Nyumba Ya tsiku la 
chimaliziro njabwino kwambiri, 
Ndipo taonani ubwino wa Nyumba 
Ya oopa Mulungu! 

31. Minda yamuyaya 
adzailowa, pansi pake Padzakhala 
pakuyenda mitsinje ndi Patsogolo 
pake, chokhumba chilichonse 
Akachipeza mmenemo (popanda 
kuchivutikira); Umo ndi momwe 
Mulungu amawalipirira Omuopa 

(iye), 

32. Amene miyoyo yawo 
angelo amaitenga Iwo ali 
abwino,(angelo) akunena kuti: 
"Mtendere uli pa inu, lowani 


















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 I 561 I \ t *>» 



\ \ Jj»Ji djj~> 



kumunda Wamtendere chifukwa 
cha (zabwino) zija Zomwe mudali 
kuzichita." 

33. Kodi akuyembekezera 
china, awa Osakhulupirira, 
posakhala kuti angelo awadzere 
Ndikuwaononga; kapena kuti 
liwadzere Lamulo la Mbuye wako 
(lakuwalanga)? Momwemo ndi 
m'mene adachitiranso omwe 
Adalipo patsogolo pawo. Koma 
Mulungu Sadawachitire choipa 
koma adadzichitira Okha choipa. 

34. Choncho, zoipa za zomwe 
adachita Zidawapeza, ndipo 
Chilango chidawazinga Pa zomwe 
ankazichita mwachipongwe. 

35. Ndipo aja Amshirikina 
akuti: "Mulungu Akadafuna, 
sitikadapembedza chilichonse 
Kusiya lye, ife ngakhale makolo 
athu; Ndiponso palibe chomwe 
tikadachiyesa Choletsedwa 
popanda lamulo Lake." 
Momwemo ndimo adachitiranso 
aja omwe Adalipo patsogolo pawo. 
Kodi atumiki Ali ndi udindo 
winanso, osati kufikitsa Uthenga 
woonekera (womveka?) 

36. Ndipo ndithu, kumtundu 
uliwonse tidatumiza Mtumiki 
(amene amawauza kuti): 
"Pembedzani Mulungu, ndi 
kumpewa (Iblis) woipa: "Choncho 
alipo ena mwa Iwo omwe 



e^teS 












I** *'**>>. 'fix /' ><>>9> < 



Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 562 > * *>* 



> % >Ji Ojj- 



Mulungu adawaongola, ndipo 
alipo Ena mwa iwo omwe 
kusokera kudatsimikizika Pa iwo. 
Choncho yendani padziko 
ndikuyang'ana (Kuti) kodi adali 
bwanji Mathero a otsutsa. 

37. Ngati uwumirira kwambiri 
kuti uwaongole Komatu Mulungu 
saongola Yemwe akusokeretsa 
(Ena), ndipo sadzapeza 
wowathangata. 

38. Ndipo iwo adalumbirira 
m'dzina la Mulungu, kulumbirira 
kwawo kwamphamvu (Kuti) 
Mulungu sadzaukitsa amene afa; 
Nchotani (kuti asawaukitse?) Hi 
ndi Lonjezo lokakamizika kwa lye, 
(kuwaukitsa Ndi kuwalipira); 
koma anthu ambiri sadziwa. 

39. (Adzawaukitsa) kuti 
Awafotokozere za Zomwe adali 
kusiyana Ndi kuti amene 
Sadakhulupirire Adziwe kuti 
ndithu iwo adali abodza. 

40. Ndithu liwu Lathu 
pachinthu chimene Tikuchifuna 
kuti chichitike ndikuchiuza Basi 
kuti,"Chitika," ndipo 
chimachitikadi. 

41. Ndipo omwe adasamuka 
chifukwa Cha Mulungu (kusiya 
midzi yawo) pambuyo 
Poponderezedwa (kumeneko,) 
ndithu Tiwakhazika mwaubwino 



*&^%&&&g 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 I 563 I \ t *jk-\ 



\ 1 J^cJi djj-i 



padziko Lapansi; ndipo malipiro a 
tsiku La chimaliziro (omwe 
akuwayembekezera), Ngakulu 
zedi, akadakhala akudziwa (Awa 
oipa). 

42. (Amene adzapeza zimenezi, 
ndi) omwe Adapirira ndi kutsamira 
kwa Mbuye wawo. 

43. Ndipo patsogolo pako 
(aneneri) omwe Tidawatuma 
adalinso amuna, omwe 
Tidawavumbulutsira 
chivumbulutso. Choncho afunseni 
eni chikumbumtima (Za 
m'Mabuku a Mulungu akale) ngati 
Inu simukudziwa. 

44. (Tidabwera) ndi zisonyezo 
Zoonekera pamodzi ndi mabuku; 
Ndipo takuvumbulutsira ulaliki 
kuti Uwafotokozere anthu Zomwe 
zavumbulutsidwa Kwa iwo kuti 
aganizire. 

45. Kodi adziika pachitetezo, 
amene Akuchita ndale zoipa, kuti 
Mulungu Sangawakwirire ndi 
nthaka, kapena Chilango 
kuwadzera kuchokera komwe 
Sadali kukudziwa (sadali 
Kukuyembekezera)? 

46. Kapena (Mulungu) 
kuwathira dzanja Mkuyenda 
kwawo kwa uku ndi uko? Pom we 
iwo sangathe kumulepheretsa 
Mulungu kuchita chomwe wafuna 
pa iwo. 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



564 \ t *>» 



> 1 J*dl 5^ 



47. Kapena kuwalanga uku ali 
ndi mantha Oyembekezera 
chilango (pakulanga 
M'modzim'modzi kufikira onse 
atatha)? Ndithu, Mbuye wanu 
Ngodekha Ngwachisoni. 

48. Kodi sadaone chinthu 
chilichonse (molingalira) 
M'zimene Mulungu adalenga 
zomwe zithuzi Zake zimazungulira 
kudzanjadzanja ndi Kumanzere, 
kulambira Mulungu uku zili 
Zodzichepetsa kwa lye? (Nanga 
iwo Osakhulupirira akudzikweza 
chotani pamaso pa Mulungu?) 

49. Ndipo zimalambira 
Mulungu zonse Zakumwamba ndi 
zapansi, Nyama ndi angelo; Iwo 
sadzikuza (pamapemphero). 

50. Amaopa Mbuye wawo 
Yemwe ali pamwamba Pawo; 
ndipo amachita zokhazo zomwe 
Alamulidwa. 

51. Ndipo Mulungu wanena: 
"Musadzipangire Milungu ina iwiri. 
Ndithudi, lye ndi Mulungu mmodzi. 
Choncho opani Ine ndekha". 

52. Zonse zakumwamba ndi 
pansi nza lye, Ndipo kumumvera 
ndi kumugonjera nkwake Nthawi 
zonse. Kodi muopa wina amene 
sali Mulungu? 

53. Ndipo mtendere wonse 
umene muli nawo Udachokera kwa 



o> 



&&®t&fi^ 









Sri'**" 9 --< 9*9)4, S&y 






Siirat 16. Al-Nahl Juzu 14 565 1 £ *>» in J~J» Sj^ 



Mulungu (koma inu Simuthokoza) 
ndipo masautso akakukhudzani, 
lye ndi amene Mumamulirira; 

54. Koma akakuchotserani 
masautso, Pompo gulu lina la mwa 
inu limamphatikiza Mbuye wake 
(ndi mafano). 

55. Ncholinga choti akane 
mtendere umene Tawapatsa, 
choncho sangalalani pang'ono, 
Posachedwapa mudziwa (mapeto a 
zochita Zanu). 

56. Ndipo gawo la zomwe 
tawapatsa akuiikira (Milungu 
yawo yabodza) yomwe siizindikira 
Chilichonse. Tallahi, 
(ndikulumbira Mulungu,) ndithudi, 
mudzafunsidwa Pazimene 
munkapeka. 

57. Ndipo (mwaumbuli) 
akumuikira Mulungu Ana aakazi 
(ponena kuti adabereka ana 
Aakazi) Subuhana! (Way era 
Mulungu Kuzimenezi!) Ndipo iwo 
(eni) Amadzifunira amene 
amawakonda (Omwe ndi ana 
achimuna)! 

58. Ndipo mmodzi wawo 
akauzidwa nkhani Ya (kuti 
wabereka) mwana wamkazi 
Nkhope yake imada, ndipo 
amadzala Ndi madandaulo. 

59. Amadzibisa kwa anthu 
chifukwa Chankhani yoipa imene 



$G&g*88WZ' 



'&&$%&&\z&<& 






^W^0^^ 









»t\*i'\»> \*% x sit'"'' 









Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



566 



U *>i 



) *\ J*cJ» Sjj* 



wauzidwa (Nayamba kulingalira) 
kodi akhale Naye pamodzi 
ndikuyaluka (pamaso pa Anthu), 
kapena angomkwirira m'dothi (Ali 
moyo)? Mverani! Ndi choipa 
Kwabasi chiweruzo chawo. 1 

60. Kwa awo amene 
sakhulupirira za Tsiku la 
chimaliziro, ali ndi mbiri Yoipa; 
koma Mulungu ali ndi mbiri 
Zapamwamba; ndipo lye 
Ngwanyonga, Ngwanzeru zakuya. 

61. Ndipo Mulungu akadakhala 
akulanga anthu (Mwachangu) 
pazolokwa zawo, Sakadasiya 
ngakhale nyama imodzi 
Pamwamba panthaka; koma 
Akuwachedwetsera (chilangocho) 
mpaka Panthawi yoikidwa; ndipo 
ikadzadza Nthawi yawoyo, 
sangathe kuichedwerera Ngakhale 
ola limodzi; ndiponso sangathe 
Kuifulumirira (ngakhale ola 
limodzi.) 

62. Ndipo akumuikira Mulungu 
zimene (iwo) Akuzida (omwe ndi 
ana aakazi Pomati Mulungu 
adabala ana aakazi), Ndipo 



* I'ii 















>^J£ 



t)l^ 



Ophatikiza Mulungu ndi mafano adali kuda ana aakazi. Kubala mwana 
wamkazi amachiona monga chochititsa manyazi pamaso pa anthu kotero kuti 
ena mwa iwo akawauza kuti mkazi wawo wabala mwana wamkazi, 
amakamkwirira mwanayo ali wamoyo chifukwa choopa kunyozedwa pamaso 
pa anthu, pomwe iwo amawayesa angelo ngati ana aakazi a Mulungu. 
Chimene amachida, amampachika nacho Mulungu, ndipo chomwe 
amachikonda amati ndicho chawochawo. Izi nzamwano, zomwe 
osakhulupirira adali kumuyankhulira Chauta. 



Surat 16. Al-Nahl Ju/u 14 



567 



M *>» 



1 1 JmaIi 5j>- 



malirime awo akunena bodza Kuti 
iwo adzapeza zabwino (kwa 
Mulungu); palibe chikaiko, ndithu 
moto Ndi wawo, ndipo iwo 
adzasiidwa (Mmenemo). 

63. Pali Mulungu! Ndithudi 
tidatumiza (Atumiki) kumitundu 
yomwe idalipo Patsogolo pako, 
koma satana Adawakometsera 
zochita zawo (Zoipa ankaziona 
kuti nzabwino Napitiriza 
kuzichita). Choncho lye (Satana) 
ndi bwenzi wawo lero, (Koma pa 
tsiku la chimaliziro, Adzadana 
naye kwambiri), ndipo iwo 
Adzapata chilango chowawa. 

64. Ndipo sitidakutumizire 
Buku (ili) Koma kuti 
uwafotokozere zomwe 
Akusiyanirapo ndi kuti (likhale) 
Chiongoko ndi chifundo kwa anthu 
Okhulupirira. 

65. Ndipo Mulungu watsitsa 
madzi Kuchokera kumitambo, 
ndipo Akuipatsa moyo nthaka Ndi 
madziwo (pomeretsa mbewu) 
Pambuyo poti nthakayo idali 
yakufa; Ndithu m'zimenezo muli 
chisonyezo (Chosonyeza kukhoza 
kwa Mulungu) Kwa anthu amene 
amamva. 

66. Palibe chikaiko, m'ziweto 
muli Phunziro ndi lingaliro kwa 
inu. Timakumwetsani zomwe zili 
m'mimba Mwaizo, (zomwe 



W*Si#a 






*&&&& 






m^%40$& 






\99 



Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



568 



M >>» 



1 1 J~Jl 5j^ 



zimatuluka) pakati Pa ndowe ndi 
magazi, (omwe ndi) Mkaka 
woyera, wabwino wokoma kwa 

Oumwa. 

67. Ndipo kuchokera kuzipatso 
za tende Ndi mphesa, mumakonza 
zakumwa Zoledzeretsa (zomwe 
nzoletsedwa) Ndikupezanso riziki 
labwino (M'zipatsozo); ndithudi 
m'zimenezo Muli lingaliro kwa 
anthu oganiza Mwanzeru. 

68. Ndipo Mbuye wako 
adaizindikiritsa Njuchi kuti: 
"Dzikonzere nyumba M'mapiri, 
m'mitengo, ndi (m'ming'oma) 
Imene (anthu) anakonza; 

69. Tsono idya zipatso 
zamtundu uliwonse Ndikuyenda 
m'njira za Mbuye wako zimene 
Wazifewetsa (kuziyenda);" 
chimatuluka M'mimba mwake 
chakumwa cha utoto 
Wosiyanasiyana (uchi), mwaicho 
muli Kuchilitsa kwa anthu 
(kumatenda Ochuluka) ndithu 
m'zimenezo muli lingaliro Kwa 
anthu oganiza (zinthu) mwakuya. 

70. Ndipo Mulungu 
adakulengani, kenako 
Akukupatsani imfa (nthawi ya 
moyo Wanu ikatha); ndipo mwa 
inu alipo ena Amene 
akubwezedwa kumoyo woipa 
(Waukalamba wogwa nkumina) 
kotero Kuti asadziwe kanthu 



©' 



v&. 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



569 * i *>' 



^ 1 J^dl 5j^ 



pambuyo Pakudziwa (zambiri); 
ndithudi Mulungu Ngodziwa 
kwambiri Wokhoza (chilichonse 
chimene Afuna kuti chichitike). 

71. Ndipo Mulungu wapereka 
zopereka Zake mochuluka kwa ena 
kuposa Ena; ndipo amene 
apatsidwa Mochulukawo 
sangagawire zopatsidwa Zawo 
omwe manja awo Adzanjadzanja 
apeza (akapolo awo) kuti Akhale 
ofanana pa zopatsidwazo (Nanga 
bwanji inu mukuti Mulungu 
ngofanana ndi akapolo Ake 
Pomwe inu simufuna kufanana ndi 
akapolo Anu?) Nanga kodi 
mtendere wa Mulungu akuukana? 

72. Ndiponso Mulungu 
adakulengerani akazi amtundu 
wanu, ndipo adakupangirani Ana 
ndi zidzukulu kuchokera mwa 
Akazi anuwo; ndipo adakupatsani 
zinthu zabwinozabwino, Kodi 
akukhulupirira zachabe, ndi 
Kuchikana chisomo cha Mulungu? 

73. Ndipo akum'siya Mulungu 
Ndikupembedza zomwe 
sizingawapezere Zopatsa ngakhale 
pang'ono, Zochokera kumwamba 
ndi pansi Ndipo sizikhoza 
chilichonse. 

74. Choncho, musaponyere 
mafanizo Mulungu. Ndithudi 
Mulungu Akudziwa, pomwe inu 
simudziwa (Chinsinsi cha zinthu.) 









ill "wit ' X l '* ' '99) 9 S* 



Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



570 1 1 *>» 



^ n jjuji ojj-- 



75. Mulungu akuponya fanizo 
la (anthu Awiri: wina ndi) kapolo 
wopatidwa (Wokhala pansi 
paulamuliro wa Munthu wina); 
yemwe alibe mphamvu 
Pachilichonse; ndi (munthu) 
yemwe Tampatsa zabwino 
zochokera kwa Ife Ndipo iye 
nkupereka rizikilo mobisa Ndi 
moonekera; kodi angafanane 
(Awiriwa? Nanga bwanji 
Mukufananitsa Mulungu ndi 
mafano?) Kuyamikidwa konse 
nkwa Mulungu. Koma ambiri aiwo 
Sadziwa (kuyamika Mulungu). 

76. Ndipo Mulungu 
waponyanso fanizo la Anthu (ena) 
awiri: mmodzi ndi Bubu (wosatha 
kulankhula), alibe Mphamvu pa 
chilichonse; ndipo iye Ndi mtolo 
wolemetsa chabe Mbuye Wake; 
kulikonse kumene wamulunjikitsa, 
Sabwerako ndi chabwino 
(chifukwa cha Umbutuma wake). 
Kodi iye angafanane ndi Yemwe 
akulamula mwa chilungamo, 
Yemwenso ali panjira yolunjika? 

77. Ndipo chinsinsi cha (za) 
kumwamba ndi (Za) pansi ncha 
Mulungu yekha, (Iye ndiye Amene 
akudziwa zochitika m'menemo, 
Osati wina wake). Ndipo kuchitika 
kwa Kiyama kuli ngati kuphetira 
kwa diso, Kapena kufulumirirapo. 
Ndithudi, Mulungu Ngokhoza 
chilichonse. 



!5-*>I ir^ 4 ^ 6?v^ ^£Sj>- 









Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



571 h t *>» 



i n j^Ji Sjj- 



78. Ndipo Mulungu 
adakutulutsani m'mimba Mwa 
amayi anu pomwe simudali 
Kudziwa chilichonse; Ndipo 
adakupatsani Kumva, kuona ndi 
Mitima kuti muthokoze. 

79. Kodi saona mbalame 
mumlengalenga Zikugonjera 
(Mulungu?) palibe amene 
Akuzigwira (kuti zisagwe) koma 
Mulungu yekha. Ndithudi 
m'zimenezo Muli malingaliro kwa 
anthu Okhulupirira. 

80. Ndipo Mulungu 
adakuikirani nyumba Zanu kuti 
zikhale mokhala (mwanu) 
Ndiponso adakupangirani zikopa 
za Ziweto (kukhala zotheka 
kuzikonza) Kukhala nyumba, 
zomwe mumaziona Kuti 
nzopepuka kuzitenga panthawi Ya 
ulendo wanu ndi panthawi ya 
Kukhazikika kwanu; ndipo 
kuchokera Kubweya wake 
wautaliutali Ndi bweya bwake bwa 
manyunyu (Ung'onoung'ono), ndi 
tsitsi lake (Laziwetozo,) 
mumakonza ziwiya (Zovala) 
zosangalatsa, kwa kanthawi. 

81. Ndipo mwa zina zomwe 
Mulungu Adapanga, 
adakupangirani zodzetsa Mthunzi; 
ndipo adakupangirani Mokhala 
kumapiri (monga mapanga 
Akuluakulu). Adakupangiraninso 






9 &$&jft£$Je& 



Kf ' *t~ 9 ^< 9 ^'tl \ "* i \* 






Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



572 



M tfr\ 



\ *\ JjnJl 5jj-- 



Nsalu (zathonje ndi ubweya) 
Zokutetezani kukutentha (ndi 
kuzizira), Ndiponso 
(adakupangirani) zovala 
(Zachitsulo) zokutetezani 
pankhondo Zanu. Umo ndi 
momwe Akukukwaniritsirani 
chisomo Chake Kuti mugonjere 
(lye). 

82. Koma ngati anyoza, basi 
palibe Udindo wina pa iwe koma 
kufikitsa Uthenga womveka 
(popanda kubisapo Kalikonse). 

83. Akuchidziwa chisomo cha 
Mulungu; Koma akuchikana, 
ndipo ambiri A iwo 
ngosakhulupirira. 

84. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
lomwe Tidzautsa mboni 
mumtundu uliwonse; Kenako 
sikudzaloledwa, kwa amene 
Sadakhulupirire, (kupereka 
madandaulo) Ndipo iwo 
sadzauzidwa kuti afunefune 
Chiyanjo cha Mulungu (Koma 
chilango basi). 

85. Ndipo amene achita zoipa 
Akadzachiona chilango 
(ndikuyamba Kudandaula ndi 
kulira), Sichidzachepetsedwa kwa 
iwo (chilangocho), Ndipo 
sadzapatsidwa mwayi wina. 

86. Ndipo amene 
ankam'phatikiza Mulungu 
Akadzawaona aphatikizi awowo 



®&&$tt&& 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



573 ht >& 



\ *\ Jj*Ji 3jj-- 



Adzati: "Mbuye wathu! Awa ndi 
Aphatikizi athu omwe tidali 
Kuwapembedza m'malo mwa 
Inu." Ndipo (aphatikizi wo 
akadzamva mawu awa) 
Adzawaponyera mawu awo 
(nkunena Kuti): "Ndithu, inu ndi 
abodza." 

87. Tsiku limenero onse 
adzadzitula kwa Mulungu; ndipo 
zidzawataikira zomwe Adali 
kuzipeka. 

88. Tsono amene 
sadakhulupirire ndi Kumaletsa 
anthu kunjira ya Mulungu 
Tidzawaonjezera chilango 
Pamwamba pa chilango chifukwa 
Chakuononga kwawo. 

89. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
lomwe Tidzautsa mboni 
mumtundu uliwonse Zochokera 
mwa iwo omwe adzawachitira 
Umboni (pa zomwe zinkachitika 
ndi Iwo;) ndipo tidzakubweretsa 
iwe Kukhala mboni pa awa (anthu 
ako;) Ndiponso takuvumbulutsira 
Buku ili Lomwe likufotokoza za 
chinthu chilichonse Lomwenso ndi 
chiongoko ndi mtendere Ndiponso 
ndi nkhani yosangalatsa Kwa 
ogonjera (Mulungu). 

90. Ndithudi, Mulungu 
akulamula (Kuchita) chilungamo, 
ndikuchita Zabwino, ndi kupatsa 
achinansi, Ndipo akuletsa zauve 






fa' 9 f 99 



&*ii*J>J 



).* \f 9 < *\ \'» ' 9 }*< 9 * 






Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



574 



M *>! 



\ 1 J~Jl i>y* 



ndi zoipa Ndi kupyola malire; 
akukulangizani Kuti muzindikire 
ndi kukumbukira. 

91. Ndipo kwaniritsani lonjezo 
(limene Mukupereka mdzina) la 
Mulungu pamene Mulonjeza, 
ndipo musaswe malonjezowo 
Pambuyo pakuwalimbikitsa; 
pomwe Mwasankha Mulungu 
kukhala mboni Yanu; ndithu, 
Mulungu akudziwa. (Zonse) 
zimene mukuchita. 

92. Ndipo musakhale monga 
mkazi yemwe Adakhulula ulusi 
wake pambuyo Pouluka 
mwamphamvu, mukukuchita 
Kulumbira kwanu pakati panu 
kukhala Kwa chinyengo, chifukwa 
chakuti gulu La mtundu wina 
nlochuluka kwambiri Kuposa gulu 
la mtundu wina (powasiya Omwe 
mudalonjezana nawo chifukwa 
Chakuwaona kuchepa, ndi 
kukagwirizana ndi Omwe 
simudalonjezane nawo chifukwa 
Chakuwaona kuchuluka); Ndithu, 
Mulungu akukuyesani mayeso 
Panjira yotere; ndipo ndithu 
patsiku la Kiyama 
adzakufotokozerani za Zomwe 
mudali kusiyana. 

93. Ndipo Mulungu akadafuna, 
ndithu, Akadakuchitani kukhala 
gulu limodzi, (Nonsenu 
mukadamumvera monga Momwe 












Surat 16. AI-Nahl Juzu 14 



575 hi *>' 



S 1 J^Ji *^ 



adawachitira Angelo, koma 
Adakupatsani ufulu kuti muchite 
Chimene mufuna); komatu 
amamulekerera Kusokera amene 
wamfuna, ndipo Amamuongola 
wamfuna; ndipo, ndithu 
Mudzafunsidwa pa zomwe 
munkachita. 

94. Ndipo musakuchite 
kulumbira kwanu kukhala Njira 
yonyengererana pakati panu 
Kuopera kuti mwendo ungaterere 
(Panjira yolungama nkukagwera 
ku moto) Pambuyo pokhazikika 
mwendowo (Panjirapo) ndi 
kukazilawa zoipa Chifukwa 
chakutsekereza kwanu (anthu) 
Kunjira ya Mulungu, ndipo 
nkupeza Chilango chachikulu 
(tsiku lachimaliziro). 

95. Ndipo musagulitse 
mapangano a Mulungu ndi mtengo 
wochepa (Wa zomwe mukupeza 
pano padziko Lapansi). Chimene 
chili kwa Mulungu, ndicho 
chabwino kwa inu Ngati 
mukudziwa. 

96. Zomwe mulinazo nzakutha 
ndipo Zili kwa Mulungu ndizo 
zosatha Ndithudi Ife tidzawapatsa 
malipiro (Aakulu zedi) amene 
adapirira Oposera zabwino zimene 
ankachita. 

97. Amene akuchita zabwino, 
wamwamuna Kapena wamkazi 



©^;8i*£#£SS*g 












Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



576 h * *>» 



\ n j*di 5j^ 



uku ali Msilamu Timkhazika ndi 
moyo wabwino (pano Padziko, ndi 
tsiku la Kiyama) Tidzawalipira 
malipiro awo mochuluka 
Kwambiri chifukwa cha zabwino 
zomwe Ankachita. 

98. Ndipo ukafuna kuwerenga 
Qur'an Dzitchinjirize ndi Mulungu 
kwa Satana wopirikitsidwa 
(ponena kuti Awudhu Billahi mina 
Shaitwani Rajim). 

99. Ndithu, iye (satana) alibe 
mphamvu pa amene 
Akhulupirira ndi kutsamira Kwa 
Mbuye wawo. 

100. Ndithudi mphamvu zake 
zili pa amene Akumusankha 
(am'lola) Kukhala bwenzi lawo 
(Mlangizi wawo) ndiponso ndi 
omwe Akumphatikiza iye (ndi 
Mulungu). 

101. Ndipo tikasintha aya 
ndikubwera ndi Ina pamalopo, 
pomwe Mulungu akudziwa 
Zimene akuvumbulutsa, akunena: 
"Ndithu, iwe ndiwe wopeka." 
Koma ambiri aiwo sadziwa 
(chilichonse). 

102. Nena: "Mzimu woyera 
(Gabriel) waitsitsa (Qur'an) 
kuchokera kwa Mbuye wako 
Mwachoonadi kuti awalimbikitse 
Nayo amene akhulupirira ndi kuti 
Ikhale chiongoko ndi nkhani 
Yabwino kwa amene alowa 


















® 



'9 V & 



Sural 16. Al-Nahl Juzu 14 



577 1 t *>« 



^ "V J»iJl Oj^-. 






m'Chisilamu (Amene agonjera 
Mulungu). 

103, Ndithu, tikudziwa kuti iwo 
akunena: "Pali munthu amene 
akumphunzitsa." (Koma) 
chiyankhulo cha amene 
Akumganizirayo nchachilendo, 
Ndipo ichi (chiyankhulo cha 
Qur'an) Ndi chiyankhulo cha 
Chiarabu chomveka. 

104, Ndithudi amene 
sakhulupirira aya Za Mulungu, 
Mulungu sawaongolera (Kunjira 
ya choonadi), choncho Adzapeza 
chilango chowawa. 

105, Ndithudi amene 
sakhulupirira Aya za Mulungu ndi 
amene Amapeka bodza (ndi 
kumalifalitsa Kwa anthu) ndipo 
iwowo ndiwo onama. 

106, Amene akukana Mulungu, 
pambuyo Pomkhulupirira, 
(chilango Chachikulu 
chikumyembekezera), Kupatula 
yemwe adakakamizidwa, Uku 
mtima wake utakhazikika pa 
Chikhulupiriro; koma amene 
Akutsekulira mtima wake 
Kusakhulupirira, mkwiyo wa 
Mulungu uli Pa iwo (ndipo anthu 
otere) adzapata Chilango 
chachikulu. 1 



1 Omasulira Qur'an akunena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha Ammar Bun 
Yasir. Amushirikina adamgwira ndi kumuvutitsa zedi kufikira iye adawapatsa 
chomwe iwo ankafuna kwa iye monkakamiza kutero. Anthu adati: "Ndithudi, 












Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



578 hi *>» 



S 1 J*di l^ 



107. Zimenezo nchifukwa 
chakuti iwo Adakonda moyo 
wadziko lapansi Kwambiri kuposa 
wa pambuyo Pa imfa; ndi kutinso 
Mulungu saongola Anthu 
osakhulupirira. 

108. Iwo ndi omwe Mulungu 
adawadinda M'mitima mwawo, 
m'makutu mwawo, Ndi m'maso 
mwawo (chifiikwa cha Kusimbwa 
kwawo). Ndipo iwo 
Ngonyalanyaza (malamulo A 
Mulungu) kwambiri. 

109. Palibe chikaiko chakuti 
iwo ngotaika Kwambiri pa tsiku la 
chimaliziro. 

110. Ndithudi kenako Mbuye 
wako, Kwa amene adasamuka 
pambuyo Pakusautsidwa (kufikira 
adanena Zosayenera) komanso 
nkuchita jihad Ndikupirira 
(chifukwa cha "dini",) ndithu, 
Mbuye wako pambuyo 
pazimenezo, Ngokhululuka 
kwambiri, Ngwachisoni. 

111. (Akumbutse za) tsiku 
lomwe mzimu Uliwonse udzadza 
ukudziteteza wokha (Wosalabadira 
za mwana wake, mkazi Wake ndi 






©t^l^i 



**tt 















Ammar watuluka m'Chisilamu." Mtumiki (SAW). Adati: "Ndithudi, Ammar 

ngodzaza ndi chikhulupiriro kuyambira kumutu mpaka kumapazi. Chikhulupiriro 

chasakanikirana ndi minofu ndi magazi ake". 

Zitatero Ammar adabwera kwa Mtumiki (SAW) uku akulira. Mtumiki (SAW) 

adati kwa iye: "Kodi ukupeza bwanji mtima wako?" lye adati: "Ngokhazikika pa 

chikhulupiriro." Mtumiki adati: "Ngati abwereranso iwenso bwerezanso zimene 

wanenazo." 



Surat 16. AI-Nahl Juzu 14 



579 > i *>» 



\ >\ J*Ji Sjj- 



abale ake,) ndipo mzimu Uliwonse 
udzalipidwa molingana ndi 
Zochita zake zimene unkachita, 
Ndipo iwo sadzachitidwa 
chinyengo (Pochepetsedwa 
mphoto yawo yoti Alandire.) 

112. Ndipo Mulungu waponya 
fanizo Lamudzi womwe udakhala 
mwa Mtendere, mokhazikika 
"riziki" Lake (madalitso) 
linkaudzera Mochuluka kuchokera 
malo aliwonse; Koma (mudziwo) 
udakana mtendere Wa Mulungu 
(pakusathokoza); Choncho 
Mulungu adaulawitsa Chovala cha 
njala ndi mantha Chifukwa cha 
(zoipa) zomwe (anthu Ake) adali 
kuchita. 

113. Ndipo adawadzera 
mtumiki wochokera Mwa iwo, 
koma adamtsutsa; choncho 
Chilango chidawafika uku ali 
Odzichitira okha zoipa. 

114. Idyani zimene Mulungu 
wakupatsani Zomwe zili zahalali, 
zabwino; ndipo Yamikani 
mtendere wa Mulungu Ngatidi 
mukupembedza lye. 

115. Ndithu, wakuletsani 
(kudya) zakufa Zokha, magazi 
(liwende), nyama ya Nkhumba ndi 
chimene chazingidwa Posatchula 
dzina la Mulungu. Koma amene 
wasimidwa (Nadya choletsedwa) 
Mosafuna kapena kupyoza 



®fci 



'*§& 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



580 



U *>i 



^ n Jj*J» 5jj-- 



Muyeso, (Mulungu amkhululukira) 
Ndithudi Mulungu Ngokhululuka 
kwabasi, Ngwachisoni. 

116. Ndipo musanene chifukwa 
chabodza Lomwe malirime anu 
akunena (kuti) "Ichi nchololedwa; 
ichi ncholetsedwa; (Popanda 
umboni)." Kuopera Kuti 
mungampekere bodza Mulungu. 
Ndithu, amene akupekera bodza 
Mulungu, sangapambane. 

117. Ndichisangalalo chochepa 
(cha M'dziko lapansi chimene 
chikuwachititsa Zimenezo); ndipo 
iwo Adzapata chilango chowawa. 

118. Ndipo kwa Ayuda 
tidawaletsa kale Zimene 
takusimbira. Ndipo sitidawachitire 
Chinyengo (pakuwaletsa 
zimenezo), Koma iwo okha adali 
kudzichitira Chinyengo. 

119. Kenako ndithu, Mbuye 
wako, kwa Amene achita zoipa 
mwaumbuli ndipo Nkulapa 
pambuyo pazimenezo nachita 
Zabwino, ndithudi Mbuye wako 
Pambuyo pazimenezo 
Ngokhululuka kwabasi, 
Ngwachisoni. 

120. Ndithu, Ibrahim adali 
mtsogoleri; (Chitsanzo chabwino 
kwa anthu), Womvera Mulungu, 
wopendekera Kuchoonadi ndipo 
sadali mwa Omphatikiza 
(Mulungu ndi mafano). 












Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



581 



U *>» 



\ n >Ji 5j^ 



121. (Adali) wothokoza 
mtendere Wake (Mulungu); 
Adamsankha ndipo 
Adamuongolera kunjira yolunjika. 

122. Ndipo tidampatsa zabwino 
padziko Lapansi, ndipo ndithudi, 
iye Patsiku la chimaliziro 
adzakhala M'gulu la anthu abwino. 

123. Kenako takudziwitsa (iwe 
Muhammad{SAW}) Kuti: "Tsatira 
njira (chipembedzo) Ya Ibrahim 
(yemwe adali) wokwanira 
Mkulungama, ndipo sadali mwa 
Omphatikiza (Mulungu ndi 
mafano.) 

124. Ndithudi Sabata idaikidwa 
kwa amene Adatsutsana pa za iyo 
(Sabatayo); ndithu, Mbuye wako 
adzaweruza pakati pawo Tsiku la 
Kiyama pazomwe Adali kusiyana. 

125. Itanira (anthu) kunjira ya 
Mbuye Wako mwanzeru ndi 
ulaliki wabwino; Ndipo tsutsana 
nawo mkutsutsana Kwabwino 
(osati motukwanana kapena 
Monyozana). Ndithu, Mbuye wako 
Iye Ngodziwa kwambiri za amene 
asokera Kunjira Yake, ndiponso 
Iye Ngodziwa Kwambiri za amene 
aongoka. 

126. Ndipo ngati mukubwezera 
(choipa chimene Mwachitiridwa), 
bwezerani cholingana ndi Chimene 
mwachitiridwacho koma ngati 



JlUiS^ftjSKB 



>lfi$ 















Surat 16. Al-Nahl Juzu 14 



582 



\t *>< 



\ \ J~Ji Sj^, 



Mutapitirira (posiya kubwezera), 
ndithu, Kutero ndi ubwino kwa 
opirira. 

127. Ndipo pirira. Kupirira 
kwakoko Kusakhale pachina chake 
koma Mulungu Basi. Ndipo 
usadandaule chifukwa cha Iwo, 
(iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo 
Usakhale wobanika chifukwa cha 
chiwembu Chomwe akuchita. 

128. Ndithu, Mulungu ali 
pamodzi Ndi amene akumuopa ndi 
Amenenso akuchita zabwino. 










Surat 17. Al-Isra' 



Juzu 15 



583 



>0 frjJH 



> v t\j*y\ oj^- 




Sura iyi ili ndi aya 111; idavumbulutsidwa ku Makka, 
kupatula aya 26, 32, 57 ndi aya zonse kuyambira 73 mpaka 80; 
zonsezi zidavumbulutsidwa ku Madina. 

Sura iyi yayamba ndikulemekeza Mulungu ndipo kenako 
yatchula nkhani ya Isra'a ndipo yatchulanso za uthenga wa Musa 
ndi zomwe zidachitika ndi ana a Isiraeli. 

Kenako surayi yafotokozanso za ulemerero wa Qur'an 
posonyeza anthu njira yolunjika. Ndipo yafotokozanso 
zisonyezo za Mulungu za chilengedwe zomwe zikupezeka mu 
usiku ndi mu usana. Yafotokozanso za mphoto yomwe anthu 
akalandire pa tsiku la chimaliziro molingana ndi zomwe 
adatsogoza kuchita padziko lapansi. 

Mulungu m'surayi wafotokozanso zomwe zimachititsa kuti 
mitundu ya anthu ionongeke, ndi khalidwe la munthu aliyense 
payekha, ndi zotsatira zantchito pa tsiku la chiweruzo. Ndipo 
padzanso mawu olimbikitsa kuchitira makolo zabwino, ndi 
mom we anthu angachitire ndi chuma chawo. 

Kenako msurayi mwadza malangizo khumi omwe ngofunika 
pa mtundu wa munthu. Ndipo Mulungu wakana bodza la 
opembedza mafano pa nkhani yokhudza angelo yomwe 
amawanamizira nayo. 




Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



584 



\e> frjJUi 



\ V t\j*y\ *;>*» 



Surat Al-Isra' XVII 





\ ljm& k 


fl 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Ulemerero ngwa Yemwe 
adayendetsa kapolo Wake usiku 
(umodzi) kuchokera Mu Msikiti 
Wopatulika (wa Makka) Kupita ku 
Msikiti wakutali (wa Baitul- 
Muqaddas), womwe tidaudalitsa 
ndi Kuzidalitsa zam'mphepete 
mwake; (Tidampititsa kumeneko) 
kuti timsonyeze Zina mwa 
zisonyezo Zathu; ndithu, lye 
(Mulungu) Ngwakumva , 
Ngowona ( chilichonse). 1 

2. Ndipo Musa tidampatsa Buku 
(la Taurat) Tidaliika kukhala 
chiongoko kwa Ana a Isiraeli 
(Mulungu adawauza): 
"Musadzipangire atetezi kusiya 
Ine." 

3. (Ndiponso adawauza kuti, E, 
inu eni) Mbumba ya amene 
tidawasenza pamodzi Ndi Nuhi! 
(Khalani othokoza monga Tate 
wanu.) Ndithu, iye adali Kapolo 
wothokoza kwambiri. 

4. Ndipo tidawazindikiritsa ana 
a Isiraeli m'Bukulo, kuti: "Ndithu, 



ojt^\i^3^j 



. j_iiT 












^&C£&fy$&j 



1 Mneneri Muhammad (SAW) pamene adakwezedwa kumwamba adaona 
zisonyezo zikuluzikulu za Mulungu monga Munda wamtendere, moto, mtengo 
wotchedwa Sidrat Muntaha, Angelo, Aneneri ndi zina zododometsa. 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



585 



>a fr jju» 



\ V t\j*y\ ojj^ 



Inu muononga padziko kawiri, 
ndipo Mudzapyola malire pochita 
zoipa, Kupyola malire kwakukulu. 

5. Ndipo likadzafika lonjezo 
(lakupatsidwa Chilango 
chakuononga) koyamba 
mkuononga Kuwiriko, 
tidzawakhwirizira pa inu anthu, 
Athu eni kumenya nkhondo 
mwaukali, Adzakhala 
akuzungulira mkatikati 
Mwanyumba zanu ndipo Lidali 
lonjezo lochitika. 

6. Kenako tidakubwezerani 
kupambana pa iwo (Omwe 
adakugonjetsani poyamba); ndipo 
Tidakupatsani chuma ndi ana, 
Ndikukudalitsani kukhala ndi gulu 
Lochuluka. 

7. (Tidati kwa iwo), ngati 
muchita bwino (Pomumvera 
Mulungu), ubwino ngwanu 
(Padziko lapansi ndi patsiku la 
Chimaliziro);ngati muipitsa 
(ponyoza Mulungu), kuipako kuli 
pa inu nokha. Choncho pamene 
idadza nthawi ya Lonjezo 
lachilango chomaliza, 
(Tidakutumizirani adani anu) kuti 
apereke Kunyozeka pankhope 
zanu, ndikutinso alowe Munsikiti 
monga adalowera mnthawi 
yoyamba, Ndikuti aononge 
chilichonse chimene Achigonjetsa; 
kuononga kwakukulu. 



^;<^u»3ki&js 






<&Z2\&;^% 






o* *£_ K'Xl *H '"\ *& ?'"i*\ 






Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



586 ^ * *>» 



^ v t\j*y\ *jj~> 



8. (Koma ngati mudzalungama 
mzochita zanu), Mbuye wanu 
adzakuchitirani Chifundo; ndipo 
ngati mudzabwereranso 
(Kumachitidwe anu okhota), 
tidzabwereranso (Kukulangani); 
ndipo taikonza Jahannama 
Kukhala ndende ya osakhulupirira. 

9. Ndithu, iyi Qur'an 
ikuongolera ku njira Yoongoka ndi 
kuuza okhulupirira nkhani 
Zabwino omwe akuchita zabwino, 
kuti Iwo adzalandira malipiro 
aakulu (Patsiku la chiweruzo); 

10. Ndiponso ikuuza 
omwe sadakhulupirire Za tsiku 
lachimaliziro kuti Tawakonzera 
chilango chowawa. 

11. Ndipo munthu amafulumira 
kupempha zoipa Monga 
momwenso amafulumirira 
kupempha Zabwino; ndithu, 
munthu ngwaphuma (Mzochita 
zake). 

12. Ndipo tapanga usiku ndi 
usana (mkusinthana-Sinthana 
kwake) monga zisonyezo Ziwiri 
(zosonyeza umodzi wa Mulungu 
Ndi mphamvu Zake zoposa); 
ndipo Tidachifafaniza chisonyezo 
cha usiku (Kuti chisakhale ndi 
kuunika) ndipo Chisonyezo cha 
usana tidachipanga Kuti chikhale 
ndikuunika; kuti Mufunefune 












Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



587 



>0 frj*-l 



\ V t\j*y\ 5j>- 



ubwino wochokera kwa Mbuye 
wanu, ndikuti mudziwe 
chiwerengero Cha zaka 
ndichiwerengero (cha miyezi Ndi 
masiku); ndipo chinthu chilichonse 
(Chofunika pachipembedzo ndi 
zam'dziko), Tachilongosola 
bwinobwino, Mwatsatanetsatane. 

13. Ndipo munthu Aliyense 
tammangirira Mkhosi zochita 
zake; ndipo tsiku La kiyama 
tidzamtulutsira kaundula (Momwe 
muli zochita zake); Adzampeza 
wovundukulidwa. 

14. (Kudzanenedwa kwa iye:) 
"Werenga Kaundula wako 
(kupyolera m'mphamvu za 
Mulungu ngakhale padziko lapansi 
Siunkatha kuwerenga); mzimu 
wako Ukwanira lero 

kudzi werengera. " 

15. Amene waongoka (potsatira 
njira ya Choonadi), wadzipindulira 
yekha Ndipo amene wapotoka (ku 
njira ya Choonadi), wadzitaya iye 
mwini Ndipo msenzi wosenza 
machimo sadzasenza Mtolo 
wamachimo awina. Ndipo Ife 
Siolanga (zolengedwa) kufikira 
titatumiza Mtumiki (kuti 
azidziwitse choonadi. Zikakana 
ndipomwe timazilanga). 

16. Ndipo tikafuna kuononga 
mudzi (pamene eni Mudziwo 






®s^&&#vP$$s\ 






^jX^Cj^'3 %'>)% 



Surat 17. AMsra' Juzu 15 I 588 > d *j*r\ 



\ v t\j*y\ Sjj- 



akuchita zoipa), timawalamula 
Opeza bwino a m'menemo (kuti 
asiye Zoipa). Koma akapitiriza 
kuononga Kwawo m'menemo,apo 
ndipo liwu (Lakuwaononga) 
limatsimikizidwa pa Iwo ndipo 
timauononga, kuononga 
Kwakukulu. 

17. Ndi mibadwo yochuluka 
imene tidaiononga Pambuyo pa 
Nuhi! Ndipo akukwanira Mbuye 
wako kudziwa bwinobwino ndi 
kuona Bwinobwino uchimo wa 
akapolo ake. (Palibe chobisika kwa 
lye M'zochita chita za anthu). 

18. Amene afuna zosangalatsa 
za m'dziko Zachangu 
(ndikumaikirapo mtima pa izo,) 
Timpatsiratu mwachangu padziko 
Lapansi chimene tikufuna Kwa 
amene tafuna (kumpatsa;) koma 
(tsiku Lachimaliziro) tamkonzera 
Jahannama Adzailowa ali 
wonyozeka, wopirikitsidwa Apa 
ndi apo. 

19. Ndipo amene afuna Tsiku 
lachimaliziro (Mzochita zake) 
ndikuligwirira Ntchito yake 
yeniyeni uku Ali msilamu, iwowo 
Khama lawo lidzakhala 
lolandiridwa. 

20. Onse awa, (abwino ndi 
oipa), timawapatsa Awa ndi awa 
mwazopatsa za Mbuye wako; 















dssQs3x^%$4$i 



Surat 17. Al-Isra' 



Juzu 15 



589 



>0 frj*-! 



> V t\j*f\ 5j>- 



Ndipo zopatsa za Mbuye Wako 
sizotsekerezedwa (Kuti zisamfike 
kapolo Wake). 

21. Taona (ndi diso lolingalira) 
m'mene Tawasiyanitsira mkupeza 
bwino, ena nkukhala Pamwamba 
pa anzawo (pachuma ndi pamoyo 
Wangwiro); ndipo pa tsiku la 
chimaliziro Kusiyana kwawo pa 
masitepe ndi ulemerero, 
Nkwakukulu kwabasi. 

22. Usadzipangire mulungu 
wina ndi kumphatika Kwa 
Mulungu; kuti ungadzakhale 
wodzudzulidwa (Kwa Mulungu) 
ndikusiidwa wopanda m'thandizi. 

23. Ndipo walamula Mbuye 
wako kuti musapembedze (Wina) 
koma lye yekha, ndi kuti Muchitire 
zabwino makolo (anu). Ngati 
M'modzi waiwo afika msinkhu 
waukalamba Uli naye, kapena 
onse awiri, Usawanenere,mawu 
amnyozo Ndiponso Usawakalipire 
koma yankhula nawo Ndi mau 
aulemu. 1 

24. Ndipo afungatire ndi phiko 
lodzichepetsa Powachitira chisoni, 












$0S&$SM^J*£ 



M'ndimeyi Mulungu akulamula anthu Ake kuti apembedze lye yekha; 
asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, 
mwezi, nkhalango zowirira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma 
chikhulupiriro chathu chikhale mwa Mulungu yekha. Tikafuna kudziteteza 
tidziteteze ndi Mulungu. Ndiponso Mulungu watilamula kuchitira zabwino 
makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma 
tiwanenere mau aulemu. 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



590 



>0 ij±\ 



1 V *lj^1 5jj-- 



ndipo nena: "Mbuye Wanga 
achitireni chisoni (makolo anga) 
Monga momwe ankandilerera ku 
ubwana." 

25. Mbuye wanu akudziwa 
kwambiri zomwe zili M'maganizo 
mwanu; ngati muli ofuna Kuchita 
zabwino, (kwa makolo anu lye 
Akudziwa. Ndipo ngati 
mutawalakwira, Kenako 
ndikulapa), ndithu, lye ndi Mwini 
kukhululukira otembenukira kwa 
lye. 

26. Ndipo mnansi wako, 
masikini ndi Wapaulendo (yemwe 
alibe Choyendera) mpatse gawo 
lake (La chuma chako) ndipo 
usamwaze (Chuma chako) 
mosakaza. 

27. Ndithu omwaza chuma 
mosakaza, ndi Abale a satana 
(otsatira satana), Ndipo satana 
ngosathokoza Kwa Mbuye wake. 

28. Ndipo ngati ukuwapewa 
opempha (Pamene ulibe 
chowapatsa) pamene Ukufunafuna 
chifundo cha Mbuye Wako 
chomwe ukuchiyembekezera, nena 
Kwa iwo mau ofewa (ponena kuti: 
"Ndikapeza chokupatsani, 
ndikuninkhani.") 

29. Ndipo mkono wako 
usaukhalitse Ngati kuti 
wamangidwa kukhosi kwako, 



*&&$%&$ 












^JflSi-^MK 



Surat 17. AI-Isra' Juzu 15 



591 > * *>» 



>v *\j*y\ 5jj-- 



Ndiponso usautambasule 
mosayenera, Ungadzakhale 
wodzudzulidwa ndiwosowa. 1 

30. Ndithu, Mbuye wako 
amamtambasulira Riziki amene 
wamfuna, ndikulichepetsa (Kwa 
amene wamfuna). Ndithu, lye 
Ngodziwa bwino; wopenya bwino 
za Akapolo Ake. 

31. Ndipo musaphe ana anu 
poopa umphawi. Ife ndi amene 
tikuwapatsa iwo ndi Inu. Ndithu, 
kupha anawo ndi Tchimo lalikulu. 

32. Ndipo musachiyandikire 
chiwerewere; Ndithu, (icho) ndi 
uve (chonyansa chachikulu), 
Ndiponso ndi njira yoipa. 

33. Ndipo musaphe munthu 
amene Mulungu waletsa 
(Kumupha) koma mwachoonadi 
(Poweruza oweruza zakuphedwa 
ngati Utam'gwera mulandu 
woyenera kuphedwa). Ndipo 
amene waphedwa mopanda 
chilungamo, Tapereka mphamvu 
kwa mlowammalo wake (Wa 
wophedwayo atafuna 
angamuphenso Kapena kumsiya 
ndikulandirapo dipo); Koma 
asapyole malire mukuphako. 



4$tt&&^3tifty^' 






^ T7 ^ 












1 Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya 
kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza 
koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu 
aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana. 



Surat 17. Al-Isra' 



Juzu 15 



592 



^a *>i 



\ V $\jJ$\ oj^- 



Ndithu, lye ngothandizidwa ndi 
Shariya. 

34. Ndipo musachiyandikire 
chuma cha wamasiye (Pochidya 
mosayenera) koma pokhapokha 
M'njira yomwe ili yabwino, 
kufikira Anawo atakula, (apo tsono 
apatsidwe Chuma chawocho); 
ndipo kwaniritsani Lonjezo, 
popeza lonjezo lidzafunsidwa 
(Tsiku la Kiyama). 

35. Ndipo kwaniritsani mlingo 
pamene Mulinga, ndipo yesani ndi 
sikelo Zabwino, zimenezo ndi 
zabwino (kwa inu) Ndiponso 
mathero (ake) ngabwino. 

36. Ndipo usazitsate (pongo 
Ziyankhulayankhula Kapena 
kuzichita) zomwe Sukuzidziwa; 
ndithu Makutu, maso Ndi mtima 
zonsezo Zidzafunsidwa. 

37. Ndipo usayende padziko 
modzitukumula; Ndithu, iwe 
sungang'ambe nthaka Ndiponso 
sungalifikire phiri M'kutalika. 

38. Zonsezi kuipa kwake 
Nkonyansidwa kwa Mbuye wako. 

39. Izi ndi zina mwa za nzeru 
zomwe Mbuye wako 
wakuvumbulutsira. Usakhale Ndi 
mulungu wina ndi kumphatikiza 
Kwa Mulungu, kuti 
ungadzaponyedwe ku Jahannama 












Siirat 17. Al-Isra' Juzu 15 I 593 I \ o ^\ w t\j*y\ 5^ 



uli wodzudzulidwa ndi 
Wopirikitsidwa apa ndi apo. 

40. Kodi Mbuye wanu 
wakusankhirani ana Aamuna, 
ndipo mwini wadzipangira Ana 
aakazi achingelo? Ndithu, Inu 
mukunena liwu lalikulu. 

41. Ndipo ndithu, talongosola 
lamulo la chinthu Chilichonse 
mwatsatanetsatane m'Qur'an Iyi 
kuti akumbukire, ndipo (oipa) 
Siikuwaonjezera (china) koma 
Kuida ndi kuithawa. 

42. Nena: "Pakadakhala 
milungu ina pamodzi Ndi 
Mulungu, monga momwe 
akunenera, Ikadafuna njira 
yomufikira (Mbuye) Mwini 
mpando wa chifumu (ndi Kumthira 
nkhondo)". 

43. Wayera ndipo watukuka 
Mulungu ku zimene akunenazo; 
Kutukuka kwakukulu (kwabasi). 

44. Zonse zakumitambo isanu 
ndi iwiri Ndi nthaka ndi 
zam'menemo, Zikulemekeza lye; 
ndipo palibe Chilichonse koma 
chikumlememekeza ndi 
Kumtamanda; koma inu 
simuzindikira Kulemekeza 
kwawo! Ndithujye (Mulungu) 
Ngodekha, Ngokhululuka. 

45. Ndipo ukamawerenga 
Qur'an (zikukhala Ngati) taika 






$££& 






m 









{^^^£>^2^Q\j^\^^\^ 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



594 



> o ftjA-i > V fri^i 5jj- 



chotchinga Pakati pako ndi pakati 
pa amene Sadakhulupirire za tsiku 
lachimaliziro. 

46. Ndipo (ngati) taika 
zitsekerero M'mitima mwawo kuti 
angaizindikire, Ndipo (ngati) 
mmakutu mwawo muli Kulemera 
kwa ugonthi. Ndiponso 
ukamtchula M'Qur'an Mbuye wako 
yekha, iwo Akutembenuka ndi 
misana yawo moipidwa. 

47. Ife tikudziwa chifukwa 
chomwe akuimvetsera (Qur'an), 
pamene akukumvetsera Ndi 
pamene akunong'onezana, awo 
Achinyengo, (ndikuuza Asilamu 
kuti) "Inu simutsatira (wina) koma 
munthu Wolodzedwa." 

48. Ona momwe akukufanizira 
ndi Mafanizo abodza. (Nthawi zina 
akuti Ndiwe wolodzedwa, nthawi 
zina akuti Ndiwe mfiti!) choncho 
asokera, Ndipo sangathe kupeza 
njira (Yeniyeni). 

49. Ndipo akunena: "Kodi 
tikadzakhala mafupa Odukaduka, 
tidzaukitsidwanso Kukhala 
zolengedwa zatsopano?" 

50. Nena: "Khalani miyala 
kapena Zitsulo, 

51. Kapena cholengedwa 
chilichonse Mwazomwe zikuoneka 
kuti nzovuta Kwambiri m'mitima 
mwanu (m'maganizo Mwanu), 



^m>%*w& 



®l 


















Surat 17. AMsra' Juzu 15 



595 p**j*-» 



> V *ij-»)h 5j>- 



(ngakhale mutakhala zimenezo, 
Mudzaukitsidwa)" pamenepo 
anena: "Ndani adzatibweza?" 
Nena: "Yemwe adakulengani 
pachiyambi" Pamenepo 
adzakupukusira mitu yawo 
Ndikunena: "Zichitika liti 
Zimenezo?" Nena: "Mwina zili 
pafupi!" 

52. "(Zidzakhala) pa tsiku 
lomwe Adzakuitanani (Mulungu), 
ndipo inu Mudzayankha 
momuyamikira, ndipo 
Mudzaganizira kuti simudakhale 
(Padziko lapansi) koma (kwa) 
nthawi Yochepa." 

53. Ndipo auze akapolo Anga 
kuti (Nthawi zonse) azinena 
zomwe zili Zabwino; chifukwa 
satana Amakhwirizira mikangano 
pakati Pawo; ndithu, satana kwa 
munthu, Ndi mdani woonekera. 

54. Mbuye wanu akukudziwani 
bwino. Ngati afuna akuchitirani 
chisoni (Mukatembenukira kwa 
lye), ndipo Ngati afuna, 
akulangani (Mukapitiriza 
kumnyoza); ndipo Sitidakutumize 
kuti ukhale kapitawo Wawo. 

55. Ndipo Mbuye wako 
Akuwadziwa bwino Onse ali 
kumwamba ndi pansi, Ndithu, 
tawapatsa ulemerero Wambiri 
aneneri ena kuposa ena. Ndipo 
Daud tidampatsa Zaburi. 


















Siirat 17. Al-Isra' Juzu 15 



596 



>0 tjJUl 



\ V s.\jJ)\ 3jj- 



56. Nena: " Aitaneni amene 
munkawatcha Kuti ndi mulungu 
kusiya lye (Mulungu) Kuti 
akuchotsereni Masautso sadzatha 
kukuchotserani Vuto lililonse 
ngakhale kulisintha (Kuti likhale 
chabwino)." 

57. Iwo amene akuwapempha 
(naonso) Akufunafuna njira 
yoziyandikitsira Kwa Mbuye 
wawo (ngakhale) omwe Ali pafupi 
mwa iwo (ndi Mulungu, Monga 
angelo); naonso akuyembekezera 
Chifundo Chake ndi kuopa 
chilango Chake; ndithu, chilango 
cha Mbuye wako, nchoopedwa. 

58. Ndipo sipadzapezeka mudzi 
uliwonse Koma Ife tidzauphwasula 
tsiku la Kiyama lisanadze, kapena 
tidzaulanga Ndi chilango chaukali 
(ngati uli Woyenerana ndi 
zimenezo). Izi Zidalembedwa 
m'Buku. 

59. Ndipo palibe chimene 
chikutiletsa Kutumiza zizizwa 
(zomwe Akuzipempha) koma kuti 
anthu akale Adazitsutsa. Asamuda 
tidawapatsa Ngamira yaikazi kuti 
ikhale Chizindikiro choonekera 
(chozizwitsa) Koma adaichitira 
zosayenera; ndipo Sititumiza 
zizizwa ndi cholinga China, koma 
kuchenjeza. 

60. Ndipo (kumbuka) pamene 
tidakuuza Kuti ndithu, Mbuye 



^/"*':?'M»'Ii.v4 






'**£& 






**JL*' 









yayw^a^gsts 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



597 



^o *jJU| 



y v t\j*y\ 5j^ 



wako wawazungulira Anthu 
(mowadziwa bwinobwino;) ndipo 
Sitidawachite maloto omwe 
tidakuonetsa Koma kuti akhale 
mayeso kwa anthu, (Kuti kodi 
akhulupirira kapena sakhulupirira,) 
Ndiponso (kutchula kwa) mtengo 
Wotembereredwa m'Qur'an 
(ndimayesonso Kwa iwo;) ndipo 
tikuwachenjeza, koma 
(Machenjezo athu) sakuwaonjezera 
china Koma kulumpha malire 
kwakukulu basi. 

61. Ndipo (akumbutse) pamene 
tidauza Angelo kuti: "Mulambireni 
Adam." Ndipo adamulambira 
kupatula Iblis (lye) adati:" Kodi 
ndimulambire Yemwe mwamlenga 
ndi dongo?" 

62. Adatinso (kwa Mulungu): 
"Kodi Mukuona uyu amene 
mwampatsa Ulemerero kuposa 
ine? Ngati mundipatsa Nthawi 
mpaka tsiku la Kiyama, ndithu 
Ndiononga mbumba yake (yonse) 
kupatula Ochepa basi." 

63. (Mulungu) adati: "Choka! 
Amene Adzakutsata mwa iwo, 
ndithu, Jahannama ndiyo mphoto 
yanu Mphoto yokwanira. 

64. Ndipo apusitse amene 
ungawathe mwa iwo Ndi liwu 
lako; ndipo asonkhanitsire Gulu 
lako la nkhondo la okwera 















Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



598 



>0 *j*-| 



\ V t\j*y\ Ojj- 



Akavalo ndi loyenda ndi miyendo; 
Tenga gawo lako pa chuma chawo 
ndi ana awo; Ndipo alonjeze 
(malonjezo abodza)." Koma satana 
salonjeza china koma Chinyengo 
basi. 

65. "Ndithu, akapolo Anga, 
ulibe nyonga Pa iwo." Ndipo 
Mbuye wako akukwanira Kukhala 
mtetezi (wawo). 

66. Mbuye wanu ndi Yemwe 
amakuyendetserani Zombo 
panyanja kuti munke mufunafuna 
Ubwino Wake. Ndithu, lye 
Ngwachisoni Kwa inu. 

67. Ndipo akakupezani 
masautso panyanja, Amasowa 
amene mumakhala mukuwa 
Pembedza kupatula lye (Mulungu). 
Koma akakupulumutsirani 
kumtunda, Mukutembenuka ndi 
kunyoza Mulungu, Ndithu, munthu 
ndi wokana (mtendere Wa 
Mulungu sayamika.) 

68. Kodi mukudziika 
pachitetezo ndi Chilango cha 
Mulungu (mukafika Pamtunda) 
kuti Mulungu sangakulowetseni 
Pansi mbali iliyonse ya Pamtunda, 
kapena sangakutumizireni 
Chigumula chamchenga (kapena 
miyala) Kenako inu simudzapeza 
mtetezi (Wokupulumutsani 
kuchilangocho)? 






ifj^^^f^^C^ &it*&\ 



$%&k 









^"l 



^ 









Siirat 17. Al-Isra' Juzu 15 599 1 ^^ 



\ V *lj~-?1 dj^ 



69. Kapena mwadziika 
pachitetezo kuti (Mulungu) 
sadzakubwezeraninso Mnyanjamo 
kachiwiri ndipo 

Nkudzakutumizirani chimphepo 
chaukali Ndikukumizani chifukwa 
cha Kusakhulupirira (ndi 
kusathokoza kwanu,) Kenako inu 
nkusapeza wokutetezani Kwa Ife? 

70. Ndipo ndithu, tawalemekeza 
ana a Adam; Ndipo tawapatsa 
zokwera pamtunda Ndi panyanja; 
tawapatsa zopatsa Zabwino 
kwambiri; ndipo tawapatsa 
Ulemerero kuposa zambiri 
m'zomwe Tidalenga; ulemerero 
waukulu Kwabasi. 

71. (Akumbutse za) tsiku 
lomwe Tidzaitana anthu onse 
m'dzina la mneneri Wawo; 
choncho, amene Adzapatsidwe 
akaundula awo ndi dzanja 
Lamanja,iwo adzawerenga 
akaundula awowo 
(Mwachisangalalo), ndipo 
Sadzaponderezedwa ngakhale 
pang'ono. 

72. Ndipo amene ali wakhungu 
pano (padziko Lapansi posapenya 
zizindikiro) Adzakhalanso 
wakhungu patsiku La chimaliziro, 
ndipo adzakhala Wosokera njira 
kwambiri (kumeneko). 

73. Ndipo ndithu, adatsala 
Pang'ono kukusokoneza Pazimene 






B» 















^3&AJ-^S^S& 



Surat 17. Al-Isra' 



Juzu 15 



600 



>0 lj*r\ 



W ^j*>y\ djj~- 



tavumbulutsa kwa iwe kuti 
Utipekere zina zake m'malo mwa 
izi; Pamenepo, akadakusankha 
kukhala bwenzi (Lawo). 

74. Ndipo tikadapanda 
kukulimbikitsa, Ukadapendekera 
kwa iwo, kupendeka Kwapang'ono. 

75. Tero, ndithu, 
tikadakulawitsa chilango 
Chachikulu chamoyo (wapadziko 
lapansi) Ndi chilango chachikulu 
utafa; Ndipo kenako siukadapeza 
mthandizi Wokupulumutsa kwa Ife. 

76. Ndipo padatsala pang'ono 
kuti Akusowetse mtendere 
M'dziko ili (la Makka) kuti 
akutulutse M'menemo; koma 
pambuyo Pako sakadakhala (ndi 
moyo) Kupatula (nthawi) yochepa. 

77. Chimenechi ndi 
chikhalidwe cha omwe 
Tidawatuma patsogolo pako mwa 
atumiki Athu, ndipo supeza 
kusintha Pachikhalidwe Chathu. 

78. Pemphera swala (za Farazi), 
dzuwa Likapendeka mpaka 
mumdima wausiku (Zomwe ndi 
swala za Zuhri, Asri, Maghrib ndi 
Isha), ndipo pempheranso Swala 
ya Fajir: ndithu swala ya Fajir 
amaichitira umboni (angelo). 

79. Ndipo pakati pa usiku, 
dzuka mtulo Ndi kupemhera 
swala; ilo ndipemphero Loonjeza 


















v\J^X$$ty^<$&_i 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



601 



>o t jJU| 



W^l *J>- 



paiwe, kuti Mbuye Wako 
angakuimike pamalo paulemu 
Potamandidwa (ndi zolengedwa 
zonse Pa tsiku la Kiyama.) 

80. Ndipo nena (mawu awa 
pomwe ukupemphera): "Mbuye 
wanga! Ndilowetseni, kulowetsa 
Kwabwino (paliponse pamene 
ndikulowa), Ndiponso nditulutseni, 
kutulutsa Kwabwino (paliponse 
pamene ndikutuluka); Ndipatseni 
mphamvu zochokera kwa Inu 
Zondithandiza ndi kugonjetsera 
adani". 

81. Ndipo nena: "Choonadi 
chafika, ndipo chachabe 
Chachoka; ndithu, chachabe 
ndichochoka (Ngakhale patapita 
nthawi yaitali)" 

82. Ndipo tikuitumiza Qur'an 
yomwe Imachiritsa (matenda a 
mmitima) Ndiponso ndi chifundo 
kwa okhulupirira. Komabe 
osalungama siikuwaonjezera 
(Kanthu kena) koma kuluza ndi 
kutayika. 

83. Ndipo tikampatsa chisomo 
munthu, (Monga moyo wangwiro 
ndikupeza bwino), Amatembenuka 
(ndikusiya kutikumbukira 
Ndikutipempha), ndipo amadziika 
kutali (Ndi Ife chifukwa 
chakudzitama ndikudzikuza), 
Koma masautso akamkhudza, 



*&%££& «5 















Siirat 17. Al-Isra' Juzu 15 



602 



>o *jJU| 



w *\j*y\ djj~> 



(monga Matenda ndi umphawi) 
amataya mtima Kwambiri. 

84. Nena (iwe Mneneri, kwa 
osakhulupirira A chikuraishi,): 
"Aliyense (wa ife ndi Inu) akuchita 
ntchito (zake ndikuyenda Panjira 
yake) ndipo Mbuye wanu 
Ngodziwa kwambiri za yemwe ali 
panjira Yolondola (potsatira 
choonadi)." 

85. Ndipo akukufunsa (iwe, 
Muhammad(SAW), Anthu ako 
mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za 
Mzimu. Nena: "Mzimu ndi chinthu 
Chomwe akuchidziwa Mbuye 
wanga yekha; Ndipo inu 
simudapatsidwe nzeru 
(Zozindikirira zinthu) koma 
pang'ono chabe, (Poyerekeza ndi 
nzeru za Mulungu)." 

86. Ndipo tikadafuna kufuta 
Qur'an (Pachifuwa chako) yomwe 
takuvumbulutsira, (Tikadatha 
kutero). Kenako sukadapeza kwa 
Ife Wokuimirira ndi 
kukupulumutsa, 

87. Koma (taisiya mu mtima 
mwako) chifukwa Cha chifundo 
chochokera kwa Mbuye wako; 
Ndithu, ubwino Wake pa iwe 
ngwaukulu. 

88. Nena: "Ngakhale 
atasonkhana anthu Ndi ziwanda 
(mothandizana) kuti Abwere ndi 






% 












3^uS>3iSM» 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



603 



\0 frjJH 



\ v t\j*y\ ojt* 



buku longa ili la Qur'an 
(Mkayalidwe ka mawu ndi 
matanthauzo ake), Sangathe, 
ngakhale atathandizana wina Ndi 
mnzake". 

89. Ndipo ndithu, 
tawalongosolera anthu, m'Qur'an 
Iyi; mkulongosola kwa njira 
Zosiyanasiyana ndikupereka fanizo 
Lamtundu uliwonse. Ndipo anthu 
ambiri Akukana (zonsezo) koma 
kusakhulupirira basi. 

90. Ndipo (pamene adalephera 
kubwera ndi Qur'an Yawo,) adati: 
"Sitingakukhulupirire Mpaka 
utatitulutsira kasupe wosaphwa 
M'dziko (lathu ili la Makka). 

91. Kapena ukhale ndi munda 
wazipatso Za kanjedza ndi mphesa 
(kuno ku Makka), Ndipo utulutse 
mitsinje yambiri pakati Pa 
mundapo. 

92. Kapena utigwetsere 
zidutswa za thambo Pamitu yathu 
monga momwe umatiopsezera, 
Apo ayi, um'bweretse Mulungu ndi 
Angelo (Kuti) tionane nawo 
nkhope kwa nkhope 
(Mwamasomphenya.) 

93. Kapena ukhale ndi nyumba 
ya golide, Kapena ukwere 
kumwamba. Ndipo 
Sitikukhulupirira kukwera kwako 
Pokhapokha utabwera ndi buku 





















Siirat 17. Al-Isra' Juzu 15 



604 



>o ^\ 



\ v t\j*y\ ojj- 



(lochokera Kwa Mulungu lomwe 
likulongosola za kuona Kwako), 
kuti tidziliwerenga". Nena (Kwa 
iwo): "Mbuye wanga alemekezeke 
Ndikupatukana ndi mbiri 
zopunguka! Ine sindine kanthu 
koma munthu, Mtumiki (monga 
aneneri ena) M . 

94. Ndipo palibe chimene 
(Amshirikina a M'makka) 
Chawaletsa kukhulupirira choona 
Pamene chivumbulutso 
chawadzera, Koma kunena kwawo 
(kwa umbuli) kwakuti, "Kodi 
Mulungu amatuma munthu 
kukhala Mtumiki (Wake)? 

95. Nena: "Padziko 
pakadakhala angelo 
Omayendayenda ndi okhazikika 
(m'malo Awo ndi m'nyumba 
zawo), tikadawatsitsira M'ngelo 
monga mtumiki kuchokera ku 
mwamba". 

96. Nena: "(Ngati mukutsutsa 
uthenga wanga) Mulungu 
wakwanira kukhala mboni (ndi 
Muweruzi) pakati panga ndi pakati 
panu (Zakuona kwa uthenga 
wanga kwa inu). Ndithujye 
Ngodziwa za akapolo Ake 
(Zilakolako zawo) Ngowona 
(zochita zawo). 

97. Ndipo yemwe Mulungu 
wamuongola, (Chifukwa cha 
kukonzeka kwake kwa ubwino), 












&*^j&&&$& 
*&$&&* 



<3^y t^ V^^^i&l^^ 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



605 



>o tjA-i 



\ V frlj-yi dj>- 



lyeyo ndi amene waongoka; ndipo 
amene Wamulekerera kusokera, 
(chifukwa cha kuipa Kwa 
khalidwe lake), simungampezere 
Athandizi kupatula lye (Mulungu). 
Ndipo pa tsiku la chiweruzo 
tidzawasonkhanitsa Uku 
akukokedwa ndi nkhope zawo Ali 
osapenya, osalankhula ndi osamva. 
Malo awo okhala ndi ku 
Jahannama. Nthawi iliyonse 
(motowo) ukatotobwa, 
Tidzauonjezera kwa iwo kuyaka 
mwaukali. 

98. (Chilango) chimenecho 
ndiyo mphoto Yawo chifukwa cha 
kusakhulupirira Kwawo zisonyezo 
(zomwe tidaziimika Kwa iwo), ndi 
kunena kwawo koti: M Kodi 
tikadzakhala mafupa ndi Zidutswa 
zonyenyekanyenyeka, 
Tidzaukitsidwanso kukhala 
zolengedwa Zatsopano?" 

99. Kodi (onyalanyaza) 
sadadziwebe kuti Mulungu Yemwe 
adalenga thambo ndi Nthaka 
Ngokhoza kulenga ena onga Iwo? 
Ndipo wawaikira nthawi 
(Yodziwika) yopanda chikaiko, 
(Yowaukitsira ku imfa). Koma 
achinyengo Akukana (zonsezi) 
koma Kusakhulupirira basi. 

100. Nena (kwa Amshirikina): 
"Mukadakhala kuti Muli nazo 
nkhokwe za chifundo cha Mbuye 












ly&*&3$&®& 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



606 



>o tji-i 



> V ^y 3jj-- 



Wanga, mukadachita umbombo 
(posagawira Ena) kuopa umphawi 
chifukwa munthu Ali ndi khalidwe 
loumira". 

101. Ndipo ndithu, tidampatsa 
Musa zizizwa zoonekera Zisanu 
ndi zinayi (komabe 
Osakhulupirira sadazikhulupirire). 
Afunse ana a Isiraeli pamene 
Adawadzera, Farawo adati kwa iye 
(Musa): "Ndithu, ine ndikukuona 
Iwe Musa kuti walodzedwa." 

102. (Musa) adati: "Ndithu, 
wadziwa Kuti palibe amene 
watumiza (mitsutso) Iyi kupatula 
Mbuye wathambo ndi Nthaka kuti 
zikhale chiphanula maso. Koma 
ine ndikukuona iwe Farawo Kuti 
waonongeka." 

103. Choncho (Farawo) adafuna 
kuwatulutsa m'dziko La Iguputo 
(Musa ndi ana a Isiraeli) Koma 
tidammiza iye ndi onse omwe 
adali nawo. 

104. (Musa ndi anthu ake 
tidawapulumutsa). Ndipo 
tidati,kwa ana a Isiraeli, (Pambuyo 
pommiza Farawo): "Khalani 
M'dziko (loyera la shamu); "ndipo 
Likazadza lonjezo lamoyo 
winawo, Tidzakubweretsani 
nonsenu (muli M'chipwirikiti.) 

105. Ndipo chifukwa 
chobweretsa choonadi Padziko 






tygXL'A 






&&±&m&j& 



*} 9 S\'X< - 9 i*i ' **><SJ* 9 Vfc 



^■A*S(j^J 



% 






mfoG$3y%®@p 



Surat 17. AMsra' Juzu 15 



607 



>o *j*-i 



) V ^j~-?1 5jj~- 



tidaitumiza (Qur'an); Ndipo 
mwachoonadi, Idavumbulutsidwa. 
Ndipo sitidakutume (Ndichina) 
koma kuti ukhale wouza 
(Okhulupirira) nkhani zabwino, 
ndi Wochenjeza (osakhulupirira). 

106. Ndipo Qur'an iyi taigawa 
(m'zigawo Zosiyanasiyana 
poivumbulutsa Pang'onopang'ono) 
kuti uwawerengere Anthu mwa 
chifatse Ndipo taivumbulutsa 
pang'onopang'ono (Muzaka 23). 

107. Nena (kwa osakhulupirira 
a m'Makka Mowachenjeza): 
"Ikhulupirireni (Iyi Qur'an) kapena 
musaikhulupirire, (Zonse zili 
m'chifuniro chanu.) Ndithu, amene 
adapatsidwa nzeru kale 
(Yozindikira za m'mabuku a 
Mulungu Qur'an isanadze) 
ikamalakatulidwa kwa iwo 
(Qur'aniyi) amagwa ndi zibwano 
zawo Molambira. 

108. Ndipo amanena: "Mbuye 
wathu Ngoyera! Ndithu, lonjezo la 
Mbuye wathu ndi 
Lokwaniritsidwa! " 

109. Ndipo amagwa ndi 
zibwano zawo uku akulira, Ndipo 
(Qur'an) imawaonjezera 
Kudzichepetsa. 

110. Nena (kwa Amshirikina): 
"Mpempheni Mulungu, m'dzina la 
Allah kapena Mpempheni m'dzina 



*&j$m 



^Wfl*W^?0j6 



fc**3£j 









9 9 9 f\ 






®S8g^&&#W3i$ 



Surat 17. Al-Isra' Juzu 15 



608 



>o ^\ 



> V t\jJ$\ ojj-* 



la Rahman: Kapena dzina lililonse 
limene Mungamtchulire 
(zithandizabe); lye ali nawo maina 
abwino. Ndipo Usawerenge 
(Qur'an) paswala yako Ndi mawu 
okweza, ndiponso Usatsitse mawu 
kwambiri, koma Tsata njira 
yolingana pakati Pazimenezo 
(pokweza kwambiri kapena 
Kutsitsazedi)." 

111. Ndipo nena: 
"Kutamandidwa Kwabwino nkwa 
Mulungu, Yemwe saadadzipangire 
Mwana, ndipo alibe m'phatikizi 
Mu ufumu (Wake); ndipo alibe 
Mthandizi (womthandiza) 
Mkufooka; ndipo mkuzeni, 
Kumkuza kwakukulu!" 










Surat 18. AI-Kahf Juzu 15 I 609 I >° *& ^ A ca$&i «;>* 



SURAT AL-KAHF XVIII . ^#^| j 

Sura iyi idavumbulutsidwa ku Makka kupatula aya ya 38 ndi 
ay a zomwe zayambira pa 83 mpaka kumalekezero kwake. Ndiye 
kuti aya 29 zidavumbulutsidwa ku Madina. Surayi yayamba 
ndikuyamika Mulungu wapamwambamwamba, chifukwa 
chotumiza Qur'an yolemekezeka. Ndipo yafotokoza kuti Qur'an 
udindo wake nkuchenjeza anthu oipa, ndikuuza anthu olungama 
nkhani yabwino. Komanso ikuchenjeza anthu omwe akunamizira 
Mulungu kuti adabala mwana. 

Msurayi mwatchulidwa khama la Mtumiki (SAW) 
mkufunitsitsa kwake kuti amene akuwaitanawo, akhulupirire 
Mulungu. Ndipo mwatchulidwanso nkhani ya eni mphanga 
amene adakagona mphangamo ndipo kenako nkuzutsidwamo 
pambuyo pokhalamo ali chigonere kwa zaka zikwi zitatu (300) 
ndi zaka zisanu ndi zinayi (9). 

Kameneka kadali kagulu ka Akhirisitu komwe kadathawa 
kwawo chifukwa chakupondereza kwa mfumu yawo ya 
chiroma. Ndipo panthawi yonse yatchulidwayi kaguluko kadali 
mtulo kuphanga. Kenako Mulungu adawaukitsa monga munthu 
amaukira kutulo. Izi zidachitika kuti chikhale chisonyezo 
chakuti Mulungu akhozadi kuukitsa anthu ku imfa. 

Ndipo kenako Chauta walamula Mtumiki wake (SAW) kuti 
aziiwerenga Qur'an ndikuchenjeza anthu oipa, ndikuuza anthu 
zabwino za iyo (Qur'an). Ndipo wafotokozanso mwatsatanetsatane 
momwe anthu akumunda wamtendere adzakhalira, ndi 
momwenso anthu akumoto adzakhalire. Ndipo Mulungu 
waponya fanizo la anthu awiri. M'modzi waiwo ngolemera; 
amanyadira chuma chake ndi ana ake pomwe wachiwiriyo 
amanyadira Mulungu. Ndipo Chauta wafotokoza kuti kudalirika 
kwa Mulungu ndiko kuli koona, osati chuma ndi ana. Ndipo 
walongosolanso kuti zonse za m'dziko nzakutha. Koma tsiku la 
(chimaliziro) Kiyama ndimtendere waukulu ndiponso chilango 
chopweteka. 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 I 610 I >° *>» ^ A u^» oj^* 



Mulungu msurayi watchulanso nkhani ya Musa pamodzi ndi 
munthu wabwino yemwe adapatsidwa nzeru zododometsa ndi 
Mulungu. Ndipo m'nkhani imeneyi muli chithunzi chakuti 
munthu angakhale ndi nzeru chotani, pali zinthu zambiri zomwe 
zili kutali ndi nzeru zake ngakhale munthuyo atakhala mtumiki 
wa Chauta. Koma pokhapokha Mulungu atamzindikiritsa za 
zimenezo. 

Kenako m'surayi mwatchulidwa nkhani ya Zul Qarnain 
yemwe adafika kuvuma ndi kuzambwe ndikuti iye adamanga 
chimpanda cholimba. Ndipo kenako yadza nkhani ya tsiku la 
Kiyama ndi zochitikachitika zake za tsikulo. 

Surayi yamaliza ndikufotokoza mphoto ya okhulupirira tsiku 
la Kiyama (chimaliziro) ndi kuti nzeru za Mulungu ndi mawu 
ake sizitha. Ndikufotokoza zanjira imene tingatsate pofuna 
chiyanjo Chake. 




Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



611 



>a tjA-t 



> A ui^Jl Sj^- 



Surat Al-Kahf XVIII 



'."4a\W'i 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisonl 

1. Kutamandidwa konse 
kwabwino nkwa Mulungu, Yemwe 
adatumizira kapolo Wake 
(Mtumiki Muhammad{SWA}), 
Buku (ili Lopatulika), ndipo 
Sadalikhotetse (koma m'menemo 
Muli zoona zokhazokha.) 

2. (Walichita kukhala) loongoka 
kuti Lichenjeze anthu zachilango 
Chokhwima chochokera kwa lye 
(Mulungu), Ndikuti liuze nkhani 
yabwino amene Akhulupirira 
omwe akuchita zabwino, Kuti 
adzapeza malipiro abwino. 

3. Adzakhalamo (mumtendere 
wosathawo) Muyaya. 

4. Ndikuti liwachenjeze amene 
akunena (Kuti): "Mulungu 
wadzipangira Mwana." 

5. Iwo pabodza lawolo alibe 
kuzindikira chinthu Chilichonse 
chanzeru ngakhale makolo awo. 
Lakula kwabasi liwu lomwe 
likutuluka mkamwa Mwao. Sanena 
china koma bodza basi. 

6. Mwina udziwononga wekha 
pakuwadandaulira Chikhalidwe 
chawo kuti Sakhulupirira nkhani 



5 .w*$&: 



o&£\^\&\j 



j& 












'VV-* 



<5WS3?«a3J*c^B 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



612 



> o frji-i ) A J^3\ 3jj-- 



iyi. (Iyayi! Usakhale wodandaula 
ndi zimenezo). 

7. Ndithu, Ife tazichita zomwe 
zili pamwamba Panthaka kukhala 
zokometsera nthakayo, Ndikuti 
(mwaizo) tiwayese mayeso kuti 
(ndani) Mwaiwo ali wochita 
zabwino kwambiri. 

8. Ndipo ndithu, Ife ndi Amene 
tidzazichita Zomwe zili pamenepo 
kukhala monga Nthaka yoguga 
(yopanda mmera). 

9. Kodi ukuganiza kuti eni 
phanga ndi Eni nkhani zomwe 
zidalembedwa M'mabuku, adali 
mwa zizindikiro Zathu 
zododometsa kwambiri? (Iyayi, 
zilipo zododometsa kwabasi 
Kuposa zimenezo.) 

10. Pamene anyamata 
adathawira Kuphanga nati: 
"Mbuye wathu! Tipatseni chifundo 
chochokera kwa Inu, ndipo 
tikonzereni chiongoko M'zochita 
zathu". 1 






© b^t^^^^U^^*^iSlS 






W* W ij^j <W*> Ojoj ^V^l 



1 Nkhani ya eni phanga monga momwe adaifotokozera omasulira Qur'an, idali 
motere:- 

Mfumu yomwe idapondereza anthu inkatchedwa Dikiyanusu idali mu M'zinda 
wina kudziko la Roma umene unkatchedwa Tartusi, Mneneri Isa atapita kale. 
Mfumuyi idali kuitana anthu kuti azipembedza mafano. Ndipo imapha aliyense 
wokhulupirira mwa Mulungu amene sadali kuvomereza uthenga wake 
wopotokawo kufikira chisokonezo ndi masautso zidawakulira anthu 
okhulupirira Mulungu. Anyamata omwe adali okhulupirira Mulungu ataona 
zimenezo, anadandaula kwambiri. Ndipo nkhani ya anyamata idamufika 
mfumu wopondereza anthuyo ndipo adatumiza mithenga kuti akawatenge 
anyamatawo. Anyamatawo pamene adaimirira pamaso pa mfumu, iyo 
idawaopseza kuti iwapha ngati akana kupembedza mafano ndi kukana 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 I 613 I >° *>» >A J^\ oj^ 



kupereka nsembe. Koma iwo adatsutsana nayo naonetsera poyera 
chikhulupiriro chawo mwa Mulungu. Adati: "Mbuye wathu ndi Mbuye 
wathambo ndi nthaka. Sitingapembedze mulungu wina kusiya lye". 
Mfumu idati kwa iwo: " Inu ndinu anyamata amisinkhu yochepa, choncho 
ndikukupatsani mwayi mpaka mawa kuti mukaganize bwino." Tero iwo 
adathawa usiku namdutsa m'busa yemwe adali ndi galu. M'busayo pamodzi 
ndi galu wake adawatsatira, ndipo pamene kudacha adabisala m'phanga 
lalikulu lam'phiri. Mfumu pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsatira mpaka 
kukafika kuphangalo. Koma anthu ake adaopa kulowa m'phangamo ndipo 
mfumu idati: "Atsekereni khomo laphangali kuti afere komweko ndi njala ndi 
ludzu. Ndipo Mulungu adawagoneka tulo anyamata a kuphanga aja; adakhala 
ali mtulo chigonere osadziwa kanthu mpaka padapita zaka zikwi zitatu (300) 
ndi zaka zisanu ndi zinayi (9). Kenako Mulungu adawaukitsa. Ndipo iwo 
amaganiza kuti akhala kuphangako tsiku limodzi, kapena theka la tsiku. Ndipo 
adayamba kumva njala namtuma m'modzi wawo kuti akawagulire chakudya. 
Koma adamulangiza akadzibise ndiponso akachenjere kuti anthu asamuzindikire. 
Choncho iye adapita mpaka kukafika m'mudzimo. Kuja anapeza zizindikiro za 
mudziwo zasintha. 

Palibe aliyense mwanzika zam'mudzimo amene adamdziwa. Yekha 
adadzinong'oneza "Mwinatu ine ndasokera njira yakumudzi kwathu kuja". 
Komabe adagula chakudya. Ndipo pamene adapereka ndalama kwa 
wogulitsa adayamba kuitembenuzatembenuza ndalama ija m'manja mwake. 
Adati: "Mwaipeza kuti ndalama iyi?" Choncho anthu adasonkhana 
nayang'ana ndalama ija modabwa nati: "Kodi mnyamata iwe ndiwe yani, 
kapenatu mwatulukira chuma chomwe chidabisidwa m'nthaka ndi anthu 
akale?" lye adati kwa iwo "lyayi. Ndikulumbira Mulungu, sindidapeze chuma 
chokwiriridwa m'nthaka. Iyi ndi ndalama yomwe mtundu wanga umagwiritsa 
ntchito". Iwo adati kwa iye: "Ndalamayi njakale kwambiri, m'nyengo ya mfumu 
Dikiyanusu". lye adati modabwa: "Adatani Dikiyanusiyo?" Iwo adati, "Adafa 
kalekale!" lye adati:" Ndikulumbira Mulungu, sangandikhulupirire aliyense 
zimene nditi ndikuuzeni. Ife tidali anyamata. Ndipo Mfumuyo idatikakamiza 
kupembedza mafano. Choncho tidaithawa usiku wadzulo nkupita kukabisala 
kuphanga. Tere lero anzanga andituma kuti ndikagule chakudya. Choncho 
tiyeni pamodzi kuphangalo kuti nkakuonetseni anzangawo. Iwo adadodoma 
ndi zonena zakezo nadziwitsa mfumu ya nthawi imeneyo nkhani za 
munthuyu. Mfumuyo idali yokhulupirira Mulungu. Ndipo iyo itamva nkhaniyi, 
idapita pamodzi ndi ankhondo ake ndi nzika za m'mudziwo. Atafika kuja 
pafupi ndi phangalo, anthu akuphangalo adamva phokoso ndi migugu 
yamahatchi ndipo adaganiza kuti adali ankhondo a Dikiyanusu. Choncho onse 
adaimirira kupemphera. Ndipo mfumu idalowa nkuwapeza akupemphera. 
Pamene adamaliza kupemphera mfumu idagwirana nawo chanza niiwauza 
kuti iyo imakhulupirira Mulungu, ndikuti Dikiyanusu adamwalira kalekale. 
Kenako mfumuyo idamvera nkhani yawo niidziwa kuti, Mulungu wawaukitsa 
kuti chikhale chisonyezo kwa anthu kuti Mulungu adzawaukitsa anthu akufa. 
Kenako Mulungu adawagonekanso natenga mizimu yawo iwo ali mtulo 
chomwecho. Ndipo anthu adayamba kunena: "Timange Msikiti pomwe pali 
iwowapa wopembedzamo Mulungu". 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



614 



\ o tji-i \ A Jl^\ ojj~> 



11. Tidagonthetsa makutu awo, 
(ndikugona Kosamva nako kanthu) 
kwa zaka Zambirimbiri m'phanga 

12. Kenako tidawautsa, kuti 
tiwayese (Kuti) ndani mwa magulu 
awiriwa Amadziwa kuwerengera 
nthawi imene (Anyamatawa) 
adakhala (m'phangamo). 

13. Ife tikusimbira (iwe 
mtumiki{SAW}) Nkhani zawo 
mwachoonadi; ndithu, Iwo adali 
anyamata amene Adakhulupirira 
Mbuye wawo, ndipo 
Tidawaonjezera chiongoko. 

14. Ndipo tidalimbikitsa mitima 
yawo pa Chikhulupiriro pamene 
Adaimirira (pamaso pa mfumu 
yawo Yosakhulupirira) ndikunena: 
"Mbuye wathu ndi Mbuye wa 
thambo Ndi nthaka. Ndipo 
sitipembedza Mulungu wina 
m'malo mwa lye. Ngati titatero 
ndiye kuti tanena Zoipa zopyola 
muyeso. 

15. Awa anthu athu adzipangira 
Milungu ina kusiya Mulungu, 
nanga Bwanji sakubweretsa pa 
zaiyo ( milunguyo) Umboni 
woonekera (wosonyeza kuti Iyo 
ndi milungudi)? Kodi ndani 
Wachinyengo wamkulu woposa 
yemwe Akupekera bodza Mulungu? 

16. (Adauzana pakati pawo) 
"Ndipo ngati Muwapatuka 



©bo*' ti&2 















^S^ss^j^^^ 



Siirat 18. AI-Kahf Juzu 15 



615 



>o *j*-i 



y A J14&1 5jj-- 



ndizimene akuzipembedza Kusiya 
Mulungu, thawirani kuphanga; 
Mbuye wanu akutambasulirani 
chifundo Chake 

ndikukufewetserani zinthu Zanu 
zonse". 

17. (Zidali tere) ukadakhala 
ukuliona Dzuwa pamene 
linkatuluka (ndikuyamba 
Kukwera), ukadaliona 
likulambalala Kumbali kwa 
phanga lawo, mbali 
Yakudzanjadzanja, ndipo pamene 
linkalowa Limawadutsa mbali 
yakumanzere (Popanda 
kuwalunjika) pomwe iwo adali 
Pamtetete mmenemo. Zimenezo 
ndi Zina mwa zisonyezo za 
Mulungu (Zosonyeza kukhoza 
Kwake). Ndipo Amene Mulungu 
wamuongola iyeyo ndiye 
Woongoka; ndipo amene 
wamulekerera Kuti asokere, 
simungampezere Mtetezi kapena 
muongoli. 

18. Ndipo ungawaganizire kuti 
ali maso Pomwe iwo ali mtulo, 
uku Tikuwatembenuzira mbali 
yakumanja ndi Yakumanzere (kuti 
nthaka isadye matupi awo) Ukunso 
galu wawo atatambasula miyendo 
yake (Yakutsogolo) pakhomo ngati 
Ukadawaona ukadatembenuka 
Kuwathawa; ndithu, 
ukadadzadzidwa Mantha ndi iwo. 















Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



616 



\ o *j£-i ) A ol^\ 5jj-- 



19. Ndipo momwemonso 
tidawaukitsa kuti afunsane Pakati 
pawo (zanthawi imene akhala ali 
Chigonere). Adanena wonena mwa 
iwo: "Kodi mwakhala nthawi 
yotani muli Mtulo?" Adati, 
"Takhala tsiku limodzi Kapena 
gawo la tsiku." (Ena) adati: 
"Mbuye wanu akudziwa kwambiri 
za Nyengo imene mwakhala. 
Choncho mtumeni Mmodzi wa inu 
ndindalama zanuzi za Siliva 
kumudzi ndipo akayang'ane 
chakudya Chake nchotani chomwe 
chili choyera bwino, Ndikubwerera 
nacho chakudyacho; koma izi 
Akachite mochenjera ndipo 
asamzindikiritse Aliyense za inu. ] 

20. "Ndithu iwo akakudziwani 
(pamene Mulipa), akugendani ndi 
miyala; Apo ai akubwezerani 
kuchipembedzo Chawo 
(chopotoka), zikatero ndiye Kuti 
simdzapambananso mpaka 
kalekale. 

21. (Koma anthu anazindikira 
pamene Adaona ndalama yakale), 
momwemonso Tidawazindikiritsa 
(kwa anthu) kuti Adziwe kuti 









99 '9 * 9 9' * ' ' 9?'.\ '£' ' ftf *. 



1 Omasulira Qur'an adati:- 

Adalowa kuphangako nthawi yam'bandakucha, ndipo Mulungu adawaukitsa 
madzulo. Ichi nchifukwa chake ena ankati akhala theka la tsiku poganizira kuti 
adakhalamo usana umodzi.pomwe ena amati adakhala tsiku lathunthu.Kenako 
nati Mulungu ndi amene akudziwa nyengo imene takhalamo. Ndime iyi 
ndiumboni waukulu wotsimikiza kuti mizimu ya anthu abwino sidzaona 
kutalika nyengo vokhalira m'manda. 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



617 



)o *>» 



\ A uA^Jl 3j^» 



lonjezo la Mulungu (Loukitsa ku 
imfa zolengedwa) nloona, Ndikuti 
nthawi yachimaliziro njosa- 
Kaikitsa (ndipo kumbukani) 
pamene Adakangana pakati pawo 
pachinthu Chaochi, ena adati: 
"Mangani Chomanga pa iwo (kuti 
anthu Asamadze 

kudzawasuzumira) Mbuye Wawo 
za iwo Akudziwa bwino Koma 
amene adapambana paganizo 
Lawolo adanena: "Ndithu, ife 
timanga Msikiti wa iwowa 
(paphanga lawoli)." 

22. (Ena) akhala akunena (kuti) 
adali anthu Atatu, wachinayi ndi 
galu wawo; Ndipo (ena) akuti adali 
asanu, wachisanu Ndichimodzi 
ndigalu wawo. (Akunena) 
mwakungoganizira chabe Zomwe 
sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti 
Adali asanu ndi awiri, ndipo 
Wachisanu ndi chitatu ndi galu 
Wawo. Nena: "Mbuye wanga 
ndiye Akudziwa bwinobwino 
zachiwerengero chawo Palibe 
amene akudziwa (zaiwo) koma ndi 
Ochepa chabe " Choncho 
usatsutsane Nawo za iwo, kupatula 
kutsutsana kwa Pazinthu 
zodziwika, ndipo usamfunse 
Aliyense mwa iwo za iwo. 

23. Ndipo usanene ngakhale 
Pang'ono zachilichonse Kuti, 
"Ndichitamawa." 









4jU*Ml 






&>b&§m,$'M% 






Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 I 618 I ^° *>' Uti^li 5j>- 






24. Koma (utsogoze liwu ^\i)&5$Z&&\ %$$$[ 
lakuti); Insha'llah, (Mulungu ^%< x ^^ ' ,+ >< ^ *t ' 
akafuna!)" Ndipo mukumbuke St^Qj <^dcP-*U^ 
Mbuye wako ukaiwala ponena ®!6i*jiui<^ 
kuti: "Mwina Mbuye wanga 
anditsogolera Panjira yapafupi 
pachiongoko kuposa iyi." 1 

25. Ndipo adakhala m'phanga 
lawolo (ali mtulo) Zaka zikwi 
zitatu (300) ndikuonjezera Zisanu 
ndi zinayi (9) . 

26. Nena: "Mulungu akudziwa 
bwinobwino Nyengo imene (iwo) 
adakhala; zobisika Zakumwamba 
ndi za pansi nza lye (Mulungu 
basi); taona Mulungu kuonetsetsa! 
Taona Mulungu kumvetsetsa! 
(Mulungu Ngoona chilichonse. 
Ndipo Ngwakumva chilichonse). 
Ndipo iwo alibe mtetezi Popanda 
lye (Mulungu); ndipo lye sagawira 
aliyense Udindo Wake wakulamula. 

27. Ndipo werenga zomwe 
Zavumbulutsidwa Kwa iwe za 
m'Buku la Mbuye wako, palibe 
Amene angathe kusintha mau 
Ake, Ndipo nawe sungapeze 
potsamira ndi Pothawira (kuti 
Mulungu asakupeze.) 

1 Ayuda adamufunsa Mneneri (madalitso ndi mtendere wa Mulungu zikhale pa 
iye) zankhani ya anyamata a kuphangawo. lye adayankha kuti: "Ndikuuzani 
mawa", sadanene kuti Mulungu akafuna ndikuuzani mawa." 
Choncho chivumbulutso sichidadze kwa iye ndipo anavutika kwambiri kusowa 
chowauza anthu aja. Kenako Mulungu adamuuza zoti ngati unena pa chinthu 
kuti chimenechi ndichichita mawa, nenanso mawu oti ngati Mulungu afuna. 






*riv 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



619 



\ o tjA-i \ A J^\ Sj^- 



28. Ndipo dzikakamize kukhala 
pamodzi ndi amene Akupempha 
Mbuye wawo m'mawa ndi 
madzulo uku Akufunafuna nkhope 
Yake; (chiyanjo Chake) Ndipo 
maso ako asachoke pa iwo ndi 
(Kuyang'ana ena) ncholinga 
chofuna zokongoletsa Za moyo 
wadziko lapansi; ndipo 
usamumvere Amene mtima wake 
tauiwalitsa kutikumbukira 
Ndikumangotsatira zilakolako 
zake, Ndipo zinthu zake nkukhala 
zotaika (Zosalongosoka). 1 

29. Ndipo nena (kwa 
osakhulupirirawo, kuti) "Ichi ndi 
choonadi chimene chachokera 
Kwa Mbuye wanu": Choncho 
amene afuna, Akhulupirire; ndipo 
amene afuna, (Kusachikhulupirira) 
asakhulupirire Ndithu, achinyengo 
tawakonzera moto, Womwe 
mipanda yake ikawazinga. Ndipo 
Akapempha chithandizo (chifukwa 
cha ludzu Loopsya lomwe 
likawapeza), akathandizidwa 
Popatsidwa madzi (otentha 
kwambiri) Monga madzi a chitsulo 



9 9 te*9\" '\\9' ?><&' {,'*" 






\iZ£$*>*-* 'V*<."i 






Ndime iyi idavumbulutsidwa pamene Uyaina Bun Huswaini ndi mnzake 
adadza kwa Mtumiki ndi kumpeza atakhala pamodzi ndi omtsatira 
(Maswahaba) osauka monga: Ammaru, Suhaibu ndi Bilali ndi ena onga iwo. 
Iwo adati kwa Mtumiki "Ukadawapirikitsa anthu wambawa, ndiye kuti 
tikadakhala nawe nkumamvera zimene ukulalikira. 

Koma ife tikunyansidwa ndi ulaliki wako poona kuti nthawi zonse ukukhala ndi 
anthu onyozeka amene simabwana". Choncho Qur'an idatsika kumuuza 
mtumiki kuti "Usawathamangitse anthu omwe akupempha Mulungu m'mawa 
ndi madzulo ngakhale ndi onyozeka". 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



620 



> o frjA-t \ A oi$&i ojj~- 



chosungunuka, Omwe adzasupula 
nkhope zawo. Taona Kuipa 
chakumwa! ndi kuipa malo 
wotsamira! 

30. Ndithu, amene akhulupirira 
ndi kumachita Ntchito zabwino, 
(tidzawalipira Paubwino 
wawowo), ndithu, Ife Sitisokoneza 
malipiro a amene wagwira Ntchito 
yabwino. 

31. 1 wo adzapeza minda 
yamuyaya; yomwe Pansi ndi 
patsogolo pake Pakuyenda 
mitsinje; m'menemo 
Adzawakongoletsa powaveka 
zibangiri Zagolide, ndipo adzavala 
nsalu Zobiriwira; zasilika 
wopyapyala Ndi silika wokhuthala 
uku atatsamira Makhushoni 
mmenemo. Taonani Kukhala 
bwino malipiro! Ndi pamalo 
Potsamira pokongola (popeza 
mpumulo Wabwino)! 

32. Ndipo aponyere fanizo la 
anthu awiri Mmodzi wa iwo 
tidampangira minda Iwiri ya 
mphesa ndi Kuizunguliza ndi 
mitengo Yakanjedza; ndipo pakati 
Pa iyo tidaikapo mbewu (zina). 

33. Minda yonse iwiriyi 
idapatsa Zipatso zake ndipo 
siidapungule Chilichonse mzipatso 
zake. Ndipo Pakati pake 
tidapititsapo mitsinje. 












Surat 18. AI-Kahf Juzu 15 



621 



> o *j£-t \ A J^\ 5j>- 



34. Ndipo iye adali ndi chuma 
(china) Nati kwa mnzakeyo 
mokambirana Naye: "Ine ndili ndi 
chuma Chambiri kuposa iwe, 
(ndilinso) ndi Mphamvu zambiri 
chifukwa cha Onditsatira (omwe 
ndili nawo)." 

35. Ndipo adalowa m'munda 
mwake uku Akudzichitira yekha 
zoipa. Adati: "Sindiganiza 
ngakhale mpang'ono Pomwe kuti 
(munda) uwu udzaonongeka;" 

36. "Ndiponso sindiganiza kuti 
Kiyama (chimaliziro) 
Idzachitikadi. Ngati (itapezekadi 
Kiyamayo), ine nkubwezedwa kwa 
Mbuye wanga, ndithu, ndikapeza 
malo Abwino wobwererako 
kuposa awa. (Monga momwe 
ndapezera mwayi kuno, Ukonso 
ndikapeza, ngati Kiyamayo 
Ilikodi)." 

37. M'nzake adanena kwa iye 
mokambirana naye "Kodi 
ukumukana Yemwe adakulenga 
ndi Dongo, kenako ndi dontho 
lamadzi Aumuna ndiponso 
adakupanga Kukhala munthu 
wolingana? 

38. Koma ine ndikukhulupirira 
kuti Iye ndi Mulungu basi, Iyeyo 
ndiye Mbuye Wanga, ndipo 
sindiphatikiza aliyense Ndi Mbuye 
wanga. 


















d&$&j®;&'&M 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



622 1 * *>' 



^ A ui$&! 5j^» 



39. Ndipo pamene umalowa 
m'munda wako Ukadanena kuti izi 
ndi zimene wandifunira Mulungu, 
mphamvu sizikadapezeka Koma 
kupyolera mwa Mulungu 
(Zikadakhala zabwino kwa iwe). 
Ngati ukundiona ine ndili ndi 
chuma Chochepa ndi ana ochepa 
kuposa iwe (Koma sindisiya 
kutamanda Mulungu). 

40. Mwina Mbuye wanga 
angandipatse Zabwino kuposa 
munda wakowo Ndi kuutumizira 
mliri wachiphaliwali Kuchokera 
kumwamba, Ndipo ndikusanduka 
Nthaka yoterera (yoguga). 

41. Kapena madzi ake 
nkumangophwa Kotero kuti 
sungathe Kuwapeza". 

42. Tsono mliri unagwa pa 
Zipatso zakezo (ndikuziononga 
Motheratu), ndipo adayamba 
kutembenuza Manja modandaulira 
Zomwe adaonongera m'menemo; 
(mindayo) Mitengo yake itagwera 
pansi. Ndipo adati: "Kalanga Ine! 
Ndikadapanda kumphatikiza 
Mbuye wanga ndi aliyense 
(Zoterezi sizikadachitika.") 

43. Ndipo sadakhale ndi anthu 
omthangata Pamene Mulungu 
adamtaya, ngakhale iye Mwini 
sadadzithandize. 















Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 I 623 I ^ ° tjk-\ \ A Ji^\ 5jj~- 



44. Pamalo potere chitetezo 
chimakhala Cha Mulungu yekha 
woona, (Yemwe Ngwamuyaya.) 
lye Ngolipira bwino, Ndiponso 
Wabwino (pakudza) ndi 
Malekezero abwino. 

45. Ndipo aponyere fanizo la 
moyo wadziko lapansi, Uli ngati 
madzi Amene tikutsitsa kuchokera 
kumitambo Kenako (madziwo) 
amasakanikirana ndi Mmera 
wam'nthaka (ndikuyamba kumera 
Mokongola), kenako (mmerawo) 
nkukhala Masamba ouma 
odukaduka omwe mphepo 
Ikuwaulutsa uku ndi uku. Ndipo 
Mulungu Ali ndi mphamvu 
pachilichonse. 

46. Chuma ndi ana 
ndizokometsera za moyo Wa dziko 
lapansi, koma ntchito Zabwino 
zopitirira ndizo zabwino Kwa 
Mbuye wako, monga mphoto Ndi 
chiyembekezo chabwino. 

47. Ndipo (akumbutse) tsiku 
lomwe Tidzayendetsa mapiri 
(pouluka ngati Ubweya mu 
mlengalenga), ndipo Udzaiona 
nthaka ili tetetee, (Itatambasuka 
yosakhwinyata Ndi mapiri kapena 
zitunda), ndipo 
Tidzawasonkhanitsa (tsiku 
limenelo) Ndipo sitidzasiya 
aliyense mwa iwo (Oyamba ndi 
omaliza). 












> 999 \'Ml< * 9 ^9t"£iC\' 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



624 



^ © tji-l ^ A lA^3i 5j^* 



48. Ndipo adzabwera nawo kwa 
Mbuye wako Atandanda m'mizere 
(ndikuuzidwa), "Ndithu, 
mwatidzera monga tidakulengerani 
Pachiyambi (opanda nsapato, 
amaliseche Ndiponso opanda 
chilichonse chuma ndi Ana). 
Koma mumaganiza kuti 
sitikuikirani Lonjezo (ili louka ku 
imfa ndi kuweruzidwa)." 

49. Ndipo kaundula adzaikidwa 
(pamaso pawo) Ndipo udzaona 
oipa ali oopa chifukwa Cha zomwe 
zili m'menemo (mu kaundula), 
Ndipo adzanena: "Kalanga ife 
taonongeka! Ngotani kaundula 
uyu! sasiya chaching'ono Ngakhale 
chachikulu, koma zonse kuzilemba 
ndipo Adzapedza zonse zimene 
adazichita Zitalembedwa 
m'menemo. Ndipo Mbuye wako 
Sapondereza aliyense 
(pomusenzetsa zomwe sizake, 
Kapena kumchitira zomwe 
sizikumuyenera). 

50. Ndipo (kumbuka) pamene 
tidawauza Angelo: "Mchitireni 
sijida Adam (muweramireni 
Momulemekeza)." Onse adachitadi 
Sijida kupatula Iblis. lye adali 
Mmodzi wa ziwanda, ndipo 
adatuluka M'chilamulo cha Mbuye 
wake. Kodi lye ndi mbumba yake 
mukuwalola Kukhala abwenzi 
(anu) kusiya Ine, Pomwe iwo ndi 












Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



625 



>0 «j*-l 



^ a c^4^i' ojj-- 



adani anu? Taonani kuipa kusintha 
kwa anthu oipa! 

51. Sindidawachite (iwo) 
kukhala mboni Nkulenga kwa 
thambo ndi nthaka, Ngakhale 
kuwalenga kwawo ndipo 
Sindidawalole osokeretsa Kukhala 
athandizi (Anga). 

52. Ndipo (kumbukani) tsiku 
lomwe (Mulungu) Adzanena:" 
Aitaneni aja Omwe 
munkandiphatikiza nawo omwe 
Munkati (ndi milungu inzanga)" 
Choncho, adzaiitana koma 
siidzawayankha; Ndipo tidzaika 
chionongeko pakati pawo (Ndipo 
sadzakumananso). 

53. Ndipo woipa adzauona 
moto (panthawi Imeneyo) 
ndikutsimikiza kuti iwo alowa 
M'menemo. Ndipo moto wo 
Sadzapeza pouzembera. 

54. Ndipo ndithu, 
tawafotokozera anthu 
Mwatsatanetsatane m'Qur'aniyi 
fanizo La mtundu uliwonse; koma 
munthu Wapambana chinthu 
chilichonse pamakani. 

55. Ndipo palibe chimene 
chaletsa anthu Kukhulupirira 
pamene chiongoko choonadi 
Chawadzera ndikupempha 
chikhululuko Kwa Mbuye wawo, 
koma akuyembekezera Kuti 















Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



626 



>s *>H 



\ A ci$&1 Ojj-» 



chiwadzere chikhalidwe cha anthu 
Oyamba, kapena chiwadzere 
Chilango masomphenya. 

56. Ndiponso sitituma atumiki 
(ndi cholinga choti Adzetse 
chilango), koma kuti akhale Onena 
nkhani zabwino ndi ochenjeza. 
Ndipo amene sadakhulupirire, 
akuchitira Makani chabodza kuti 
kupyolera M'chabodzacho kuti 
achotse choonadi, ndipo Ay a 
Zanga ndi zomwe achenjezedwa 
nazo, Akuzichitira chibwana! 

57. Kodi ndani woipitsitsa 
kwabasi Woposa yemwe 
akukumbutsidwa ndi aya Za 
Mbuye wake, koma iye 
nkuzinyoza, Ndipo nkuiwala 
(zoipa) zimene manja Ake 
adatsogoza?Ndithu Ife taika 
M'mitima mwawo zitsekerero kuti 
asazizindikire. Ndiponso 
M'makutu mwawo mwalemedwa 
ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira 
kuchiongoko (choonadi), Salola 
kuongoka ngakhale pang'ono. 

58. Ndipo Mbuye wako 
Ngokhululuka kwambiri Mwini 
chifundo. Ndipo akadawathira 
Dzanja pa zoipa zomwe akhala 
akuchita, Ndiye kuti ndithu, 
akadawapatsa chilango 
Mwachangu; koma iwo ali nalo 
lonjezo Ndipo sadzapeza 
pothawira paliponse Ndikulipewa. 



®^S 



'*-'-.Ql 












Surat 18. AI-Kahf Juzu 15 | 627 \>° *> j * * Jl^S\ 5jj~> 



59. Ndipo imeneyo ndi midzi 
tidawaononga (okhalamo) Pamene 
adadzichitira zoipa okha; ndipo 
Tidawaikira lonjezo lanthawi 
yoikidwa La kuonongeka kwawo. 

60. Ndipo (kumbukani) pamene 
Musa adanena Kwa Mnyamata 
wake (Yushau Nuni), "Ndipitiriza 
kuyenda kufikira ndikafike 
Pamajiga panyanja ziwiri, kapena 
ndizingoyenda Zaka ndi zaka 
(kufikira nditakumana Naye amene 
ndikumfunayo)." 

61. Choncho pamene adafika 
pamajiga (Pa nyanja ziwirizo) 
adaiwala Nsomba yawo yomwe 
idatenga Njira yake kunka 
m'nyanja ngati una (Musa 
Adaiwala kumfunsa mnyamata 
wake Za nsombayo; naye 
mnyamata Adaiwala 
kumfotokozera Musa zomwe 
Zidachitika ndi nsombayo). 

62. Pamene adapita patsogolo, 
adauza Mnyamata wake, (kuti): 
"Tipatseni Chakudya chathu 
chamasana; ndithu Paulendo 
wathuwu takumana ndi zotopetsa." 

63. (Mnyamata) adati: "Kodi 
mwaona Pamene tidapumula paja, 
pathanthwe Ndipomwe ndidaiwala 
(kuti ndikuuzeni) Za nsombayo 
ndipo palibe Wandiiwalitsa koma 
Satana basi, kuti Ndisaikumbukire. 









3RSX2S®iJQ&®ii& 



<"'$&'-" ™ 






Surat 18. Al-Kahf Juzu 15 



628 



> o tjJUi y A Jl£3\ ojj^ 



Iyo idatenga njira Yake kunka 
m'nyanja, mododometsa." 

64. (Musa) adati : M Pamenepo 
ndi pomwe Timafuna." Choncho 
adabwerera M'mbuyo potsatira 
njira yawo (Yomweyo). 

65. Ndipo adampeza kapolo 
yemwe ndi m'modzi Wa akapolo 
athu amene tidampatsa Chifundo 
chochokera kwa Ife, (yemwenso) 
Tidamphunzitsa maphunziro 
ambiri Kuchokera kwa Ife. 

66. Musa adati kwa iye: "Kodi 
Ndingakutsate kuti undiphunzitse 
Chiongoko chomwe 
waphunzitsidwa? " 

67. Adati: "Ndithu, iwe siutha 
kupirira Nane! (Uwona zomwe 
sungathe kupirira Nazo). M 

68. "Kodi ungapirire bwanji 
ndi zinthu Zomwe sukuzidziwa 
chinsinsi chake?" 

69. (Musa) adati: "Ngati 
Mulungu afuna, Undipeza ndili 
wopirira; ndipo Sindinyoza lamulo 
lake" 

70. Adati: "Ngati unditsata 
usandifunse Za chilichonse 
(chimene uchione) kufikira Ine 
nditakuuza." 

71. Choncho onse awiri 
adanyamuka mpaka Adakakwera 
m'chombo; ndipo adachiboola 



\4? \4f< 9 9)94"rs 9 






Surat 18. Al-Kahf Juzu 16 



629 ^ 1 *>■» 



S A Jl^3\ 6jj~> 



(Chombocho). (Musa) adati: "Kodi 
Wachiboola kuti uwamize ali 
m'menemo? Ndithu, wachita 
chinthu chachikulu Choipa." 1 

72. Adati: "Kodi sindidanene 
kuti iwe Sutha kupirira nane?" 

73. (Musa) adati: 
"Usandidzudzule Chifukwa 
chakuiwala kwanga, ndipo 
Usandipatse zovuta kwambiri 
Pakhumbo langali (lofuna 
kukutsata)". 

74. Ndipo adanyamuka; mpaka 
pomwe adakumana Ndi 
m'nyamata wochepa, ndipo 
(M'neneri Khidhir) adamupha. 
Musa adati: u Ha! Waphamunthu 
wopanda cholakwa, Pomwe sadaphe 
munthu mnzake? Ndithu, Wachita 
chinthu choipitsitsa kwabasi". 

75. Adati: "Kodi sindidakuuze 
(kuti) Ndithu, iwe sutha kupirira 
nane?" 

76. (Musa) adati: "Ngati 
ndikufunsanso Chilichonse 
pambuyo pa ichi, Usandilole 
kutsagana nawe. Ndiye Kuti 
wakwaniritsa dandaulo lako pa ine". 









rifi&3$i0$$d& 



@\j&>(jf 






1 Tanthauzo lake nkuti pamene onse awiri adanyamuka adali kuyenda 
m'mphepete mwanyanja kufikira chombo chidawadutsa. Eni chombowo 
adamdziwa Khidhiru nawakweza onse awiri popanda malipiro. Atakwera 
m'chombomo Khidhiru adatenga nkhwangwa ndi kuzula thabwa limodzi la 
m'chombomo pomwe chombocho chidali pakatikati panyanja. 
Musa ataona anati: "Bwanji ukuboola chombo pomwe anthuwa atinyamula 
mwaulere?" Ndipo adatenga kasanza nkuika pomwe panachotsedwa thabwapo. 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 16 



630 



n *>» 



^ a Jl£s\ 5jj-- 



77. Choncho adamuka; kufikira 
pamene Adawapeza eni mudzi 
ndipo adawapempha Eni mudziwo 
chakudya, koma adakana 
Kuwalandira monga alendo. Ndipo 
adapezamo khoma lili pafupi 
kugwa, (Ndipo Mneneriyo) 
adaliimika. (Musa) Adati: "Ngati 
ukadafuna , ukadalandira Malipiro 
(pantchitoyi kuti tigulire Chakudya)". 

78. (Khidhiri) adati: "Awa 
ndiwo malekano Pakati pa ine ndi 
iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo 
la zomwe Sudathe kupirira nazo. 1 

79. "Tsopano chombo chija, 
chidali cha Masikini ochita ntchito 
panyanja, ndipo Ndidafuna 
kuchiononga (mwadala) chifukwa 
Patsogolo pawo padali mfumu 
yomwe Imatenga chombo 
chilichonse (chabwino) Molanda." 

80. "Ndipo mnyamata uja, 
makolo ake adali Okhulupirira, 
ndipo tidaopera Kuti 
angawachititse zoipa (makolo 
akewo) Ndi za kusakhulupirira 
(Mwa Mulungu). 

81. Choncho tidafuna kuti 
Mbuye wawo Awasinthire ndi 
wabwino kuposa iye Pakuyera, ndi 
wachifundo chapafupi (Kwa 
makolo ake.)" 















1 Mtumiki Muhammad (SAW) adati pankhani iyi ya Musa ndi Khidhiri, Mulungu 
amchitire chifundo Musa. Ndikulakalaka kuti iye akadapirira kukhala limodzi 
ndi mnzakeyo, akadaona zodabwitsa, ndipo Mulungu akadatisimbira zambiri za iwo. 



Sural 18. Al-Kahf Juzu 16 



631 



> "\ *jJ-i \ A ci^Jl «j_j-- 






82. "Tsopano chipupa chija, 
chidali cha ana awiri amasiye 
mumzindamo; Ndipo pansi pake 
padali chuma chawo (Chimene 
adawasiira bambo wawo) ndipo 
Tate wawo adali munthu wabwino 
Choncho Mbuye wako adafuna 
kuti akule misinkhu yawo ndipo 
adzadzitulutsire chuma chawocho; 
Ichi ndi chifundo chochokera kwa 
Mbuye wako. Ndipo ine 
sindidachite zinthu Zimenezi 
mwandekha. Limenelo ndilo 
tanthauzo la zomwe sudathe 
kupirira nazo". 



1 Nkhani ya Musa ndi Al-Khidhiri yomwe ikupezeka mu Sahihi Bukhari ndi 
Muslim, Ubayu bun Kaabi adailandira kuchokera kwa Mtumiki wa Mulungu 
(SAW) kuti iye adati: Ndithudi, Musa adaimirira kulalikira kwa ana a Isiraeli, 
ndipo adamufunsa kuti: "Ndani mwa anthu yemwe ngodziwa kwambiri?" lye 
adati: "Ndine." Ndipo Mulungu adamudzudzula payankho lake lotere. 
Choncho Mulungu adamuzindikiritsa iye nati: "Ndithu, ine ndilinaye kapolo 
pamajiga panyanja ziwiri yemwe ngodziwa kwambiri kuposa iwe". 
Musa adati: "E, Mbuye wanga! Ndingampeze bwanji iyeyo"? Mulungu adati: 
"Tenga nsomba, uiike muswanda (Basikete). Pamene nsombayo ikakusowe, 
ndiye kuti iye ali pamenepo." Tero Musa pamodzi ndi mnyamata wake (Yusha 
Bun Nun) adaubutsa ulendo mpaka kukafika pathanthwe. Adasamiritsa mitu 
yawo pamenepo mpaka kugona tulo. Ndipo nsomba idapiripita m'swanda 
muja, nkutuluka kukagwera mnyanja. Koma Mulungu adamanga kuyenda kwa 
madzi pamene nsombayo idagwera adangounjikana chimulu pompo. 
Pamene adauka, mnyamata uja adaiwala kumuuza zansombayo, naayenda 
usana ndi usiku kufikira mmawa mwake mwa tsiku limenelo. Musa adati kwa 
mnyamata wake, "Tipatseni chakudya chathu cham'mawa; ndithu tapeza 
zotopetsa paulendo wathupa".Adati Musa sadamve kutopa kufikira pamene 
adadutsa pamalo pomwe Mulungu adamulamulapo -. Mnyamata wake adati: 
"Kodi mwaona? Titafika pathanthwe ine ndidaiwala nkhani yansomba ija. 
Komatu palibe amene wandiiwalitsa kuikumbukira, koma Satana basi. 
Idatenga njira yake kunka m'nyanja mododometsa". Musa adati: "Pamenepo 
mpomwe timafuna". Choncho adabwerera kulondola mapazi awo mpaka 
kukafika pathanthwe lija. Apo adaona munthu atadzifundika nsalu. Musa 
adampatsa salaamu, ndipo Al-Khidhiri adati: "Yachokera kuti salaamu yotere 
m'dziko lako! Kodi ndiwe yani? Adati "Ine ndine Musa". lye adati Musa wa ana 
a Isiraeli?" Musa adavomera kuti Inde, ndadza kuti mundiphunzitse zomwe 



Siirat 18. Al-Kahf Juzu 16 I 632 I ^ *j*-» ^ A J4&1 «jj~- 



83. Ndipo akukufunsa nkhani za 
Zul-Qarnain. Auze: 
"Ndikulakatulirani zina Mwa 
nkhani zake". 

84. Ndithu, tidampatsa 
mphamvu Zokhalira padziko 
ndikumpatsa Njira yopezera 
chilichonse 

85. Choncho adatsata njira, 

86. Mpaka pomwe adafika 
Kumlowero kwa dzuwa (Ku maiko 






mwaphunzitsidwa za chiongoko". Munthu uja adati: "Ndithudi, iwe suutha 
kupirira nane chifukwa ine ndili ndi maphunziro anga omwe Mulungu 
wandiphunzitsa, amene iwe sukuwadziwa". 

Musa adati; "Undipeza ndili wopirira ngati Mulungu afuna. Sindinyoza 
chilichonse cha iwe. Al-Khidhiri adati kwa iye: "Ngati unditsatedi usandifunse 
kufikira nditakufotokozera". Choncho onse awiri adachoka nayenda 
m'mphepete mwanyanja. Chidawadutsa chombo ndipo adawalankhula eni 
chombowo kuti awanyamule. Eni chombowo adamdziwa Al Khidhiri ndipo 
adawanyamula popanda malipiro . Atakwera m'chombomo Al-Khidhiri 
adagulula thabwa la chombocho ndi nkhwangwa. Musa adati: "Nchiyani ichi; 
anthuwa atitenga popanda malipiro ndiye ukuboola chombo chawo? Kodi 
ukufuna kuti uwamize eni chombowo? Ndithudi, wachita chinthu choipa kwambiri". 
Kenaka adachoka m'chombo muja nayamba kuyenda m'phepete mwanyanja. 
Pompo Al-Khidhiri adaona mwana akusewera ndi mzake ndipo adamgwira 
mwana uja mutu wake ndikuuzula, nkumpheratu. Musa adati kwa iye: "Bwanji 
wapha munthu wosalakwa yemwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu, wachita 
chinthu chonyansa kwabasi,". Munthu uja adati; "Kodi sindidakuuze kuti sutha 
kupirira nane"? Musa adati: "Ngati ndikufunsanso chinthu china pambuyo pa 
ichi, usandilole kutsagana nawe. Apo tsono ndiye kuti kundidandaula kwako 
kwakwanira pa ine". Tero adachoka mpaka kufika pamudzi wina. Apo 
adapempha chakudya kwa eni mudziwo. Adakana kuwalandira monga 
alendo. Ndipo kenaka adapeza khoma lili pafupi kugwa, Al-Khidhiri adati ndi 
mkono wake "Ima chonchi" - polilozera ndi mkono wake. Ndipo lidaimadi 
njoo!. Musa adati: "Ha! Anthu akuti tawadzera pamudzi, ndipo sanatipatse 
chakudya sanatilandirenso ngati alendo-apatu ukadafuna ukadaitanitsa 
malipiro." Munthu uja adati: "Awa ndiwo malekano a iwe ndi ine. Komabe 
ndikuuza matanthauzo a zomwe sudathe kupirira nazo." 
Izi ndi zina zododometsa za Mulungu zomwe amazichita kupyolera m'manja 
mwa anthu Ake olungama. Ngati tidzakhala olungama ndiye kuti Mulungu 
adzatipatsa mphamvu zochita zinthu zododometsa 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 16 



633 > t *&\ 



\ A J4&1 $j^-> 



a kuzambwe), adaliona (ngati) 
Likulowa padziwe lamatope 
ambiri. Ndipo pompo adapeza 
anthu; tidati, "E, iwe Zul Qarnain! 
Alange, kapena Achitire zabwino." 

87. Adati: "Koma amene achita 
zosalungama Timulanga; ndipo 
kenako adzabwezedwa Kwa Mbuye 
wake; ndipo Akamukhaulitsa ndi 
chilango choipa. 

88. Koma amene akhulupirire 
ndikuchita Ntchito zabwino, apeza 
mphoto yabwino; Ndipo timuuza 
zomwe zili zofewa M'zinthu zathu." 

89. Kenako adatsata njira, 

90. Mpaka adafika ku mtulukiro 
kwa dzuwa (Kumaiko akuvuma). 
Adalipeza (dzuwalo) 
Likuwatulukira anthu omwe 
sitidawaikire Chowatchinga ku ilo. 

91. Momwemo, Tidali kudziwa 
bwino Nkhani zonse zomwe zidali 
ndi iye. 

92. Kenako adatsata njira, 

93. Mpaka pomwe adafika 
pakatikati pa mapiri Awiri adapeza 
pafupi Ndi mapiriwo anthu omwe 
sikudali Kwapafupi kumva 
chiyankhulo. 

94. Adati: "E, iwe Zul-Qarnain! 
Ndithu Yaajuju ndi Maajuju 
akuononga padziko. Kodi 
sikungatheke kuti tikupatse 






$&». 












Surat 18. Al-Kahf Juzu 16 



634 



\ *\ frji-l > A ci$&l djj~*> 



Malipiro kuti uike pakati pathu ndi 
Pakati pawo, chotchinga (mpanda)? 

95. (lye) adati: "Zomwe Mbuye 
wanga Wandipatsa ndi zabwino. 
Choncho Ndithandizeni ndi 
mphamvu zanu (zonse Pantchito 
imeneyi) ndiika chotchinga 
Cholimba pakati panu ndi pakati 
pawo. 

96. Ndipatseni zidutswa za 
zitsulo". Kufikira pamene 
adadzadza ndi zitsulozo Mpata 
umene udalipo pakati pa mapiri 
Awiriwo, adati: "Pemererani 
(moto)". Mpaka (chitsulocho) 
chidafiira monga Moto, adati: 
"Ndibweretsereni mtovu 
Wosungunuka ndiuthire 
pamwamba pake (Pa chitsulocho)". 

97. Choncho (Yaajuju ndi 
Maajuju) sadathe Kukwera 
pamwamba pake, ndiponso sadathe 
Kuchiboola. 

98. (lye) adati: "Ichi ndi chiflindo 
Chochokera kwa Mbuye wanga; 
koma Likadzafika lonjezo la Mbuye 
wanga (Kudza kwa Kiyama), 
adzachiswanyaswanya; Ndipo 
lonjezo la Mbuye wanga nloona. 

99. Ndipo patsiku limenelo 
tidzawasiya ena Aiwo (oipa) 
akuchita chipolowe pa ena; Ndipo 
lidzaimbidwa lipenga Pamenepo 
tidzawasonkhanitsa onse pamodzi. 












< All 9 '9* }9 9 <t. '9'9 9'9'Y^' 



Surat 18. AI-Kahf Juzu 16 



635 



n *>i 



> A ci^Jl «jj-o 



100. Ndipo tsiku limenelo, 
tidzayionetsa Poyera Jahannama 
kwa osakhulupirira. 

101. (Osakhulupirira) omwe 
maso awo adali Ophimbidwa 
pakusalabadira ulaliki Wanga, 
ndipo sadali kutha kumva (Zimene 
akuuzidwa). 

102. Kodi osakhulupirira 
akuganiza kuti Angawasandutse 
akapolo anga kukhala Atetezi 
kusiya Ine? Ndithu, Taikonza 
Jahannama kukhala malo 
Ofikirapo osakhulupirira. 

103. Nena:"Kodi tikudziwitseni 
eni Kuluza (kulephera) pazochita 
zawo?" 

104. "I wo ndi omwe khama 
lawo lataika Paumoyo wa padziko 
lapansi, pomwe Iwowo akuganiza 
kuti akuchitaZabwino". 1 

105. Iwowo ndi amene 
sadakhulupirire Zisonyezo za 
mbuye wawo, ndipo 
(Sadakhulupirire) zakukumana 
Naye. Choncho zochita zawo 



©l££ tiS^^J^*^ 












M'ndime iyi akutiuza kuti amene sadakhulupirire Mulungu, pa tsiku lomaliza 
ndiye kuti zonse zochita zawo zidzakhala zowonongeka. Ntchito zabwino za 
munthu kuti zikalandiridwe kwa Mulungu, poyamba akhulupirire Mulungu 
ndiponso akhulupirire kuti tsiku lachimaliziro lilipo. Koma ngati sakhulupirira, 
ndiye kuti zochita zake sizikayesedwa pasikelo koma akangomponya 
kung'anjo yamoto. Pankhaniyi Mtumiki (SAW) adati, "Tsiku la Kiyama 
padzabwera munthu wamtali, wakudyabwino, wakumwa zomwaimwa, koma 
kwa Mulungu adzakhala wopepuka wosafanana ngakhale ndikulemera 
kwaphiko la udzudzu". Hadisiyi adainena ndi Al -Hafizi m'buku la Fatuhul 
Bari, Volume 8 tsamba la 324. 



Surat 18. Al-Kahf Juzu 16 



636 



n *>i 



> A i^A^il Sjj-*. 



zaonongeka (Zapita pachabe), 
ndipo pa tsiku La chiweruzo 
sitidzawaikira sikero. 

106. Zimenezo, mphoto yawo 
ndi Jahannama Chifukwa cha 
kusakhulupirira Kwawo, ndipo aya 
Zanga ndi aneneri Anga 
adazichitira chipongwe. 

107. Ndithu, amene 
akhulupirira Ndikumachita 
zabwino, malo Awo ofikira 
adzakhala Kuminda ya "Firdaus". 

108. Adzakhala m'menemo 
muyaya. Ndipo Sadzafuna 
kuchokamo. 

109. Nena:"Ngakhale nyanja 
ikadakhala Inki yolembera mawu a 
Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha 
mawu A Mbuye wanga asadathe, 
ngakhale Tikadabweretsa nyanja 
ina ndikuionjezera Pa iyo 
(nyanjazo zikadatha, Mawu a 
Mulungu akalipobe)". 

110. Nena: "Ndithu, ine ndi 
munthu Monga inu, (chosiyana 
nchakuti) Ine ndikupatsidwa 
chivumbulutso (Chonena kuti) 
ndithu Mulungu Wanu ndi 
Mulungu mmodzi Yekha. Ndipo 
amene afuna kukumana ndi Mbuye 
wake, achite Zochita zabwino 
ndipo asaphatikizepo Aliyense pa 
mapemphero a Mbuye wake". 









'^iiJh'i 



Ij^CilitVrly^ >\l 






Surat 19. Maryam Juzu 16 637 ^ 1 *j*-* 



\ \ fLjA j^ 




SURAT MARYAM XIX 




Aya za Sura iyi nzaku Makka kupatula Aya ya 58 ndi 71. 
Ndipo Surayi ikufotokoza kubadwa kwa Yahaya, mwana wa 
Zakariya (A.S) 

Zakariya adapempha za mwanayo atakalamba kwambiri 
ndiponso mkazi wake adali chumba. 

M' surayi mwatchulidwanso nkhani ya Maryam ndi kubadwa 
kwa mwana wake Isa (A.S.) Ndipo yafotokozanso nkhani ya 
Ibrahim momwe ankaitanira ku Umodzi wa Mulungu, ndikuti 
iye adauza tate wake kuti asiye kupembedza mafano. 

M' surayi atchulamonso za aneneri omwe ndi ana a 
Ibrahim,monga: Ismaila ndi Isihaka. Ndipo mulinso nkhani ya 
Idrisa. Kenako Chauta wafotokozanso za magulu omwe adadza 
pambuyo pa aneneri; ena a iwo adali omvera pom we ena a iwo 
adali onyoza. 

M' surayi mwatchulidwanso kuti Janna, worn we ndi Munda 
wamtendere, idzakhala mphotho ya okhulupirira. Ndipo moto 
udzakhala mphotho ya osakhulupirira. 




Surat 19. Maryam Juzu 16 638 ^ n *j£- 



> * f.jA i ir . 



Surat Maryam XIX 






QWlt^JII^ 






M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Kaf-Ha-Ya- 'Ain-Sad . 

2. Ichi (ndi) chikumbutso cha 
chifundo cha Mbuye wako pa 
kapolo Wake Zakariya, 

3. Pamene adaitana Mbuye 
wake, Kuitana kwa chinsinsi. 

4. Adati: " E Mbuye wanga! 
Ndithu, mafupa Anga afooka, 
ndipo mutu wanga Wayaka 
(ukung'anima) Ndi imvi; sindidali 
watsoka Pokupemphani Mbuye 
wanga (koma nthawi Iliyonse 
ndikakupemphani 

Mumandi vomereza) ] 

5. "Ndipo ndithu, ine 
ndikuopera abale anga (Kuononga 
chipembedzo) pambuyo panga; 
Ndipo mkazi wanga ndi chumba; 
choncho Ndipatseni (mwana) 
mlowammalo wanga Wochokera 
kwa Inu, 

6. Adzandilowe chokolo (pa 
nzeru za Utsogoleri ndi uneneri) 
ndikulowanso Ufumu wa banja la 
Yakubu; Ndipo Mbuye wanga 



1 Apa tanthauzo lake nkuti: "E, Mbuye wanga! Palibe pamene mudalitaya 
pachabe pempho langa koma mudandizoloweza kuti ndikakupemphani 
mumandipatsa zomwe ndapempha. Choncho yankhaninso pempho langali." 









01 



Surat 19. Maryam Juzu 16 



639 



n tjk-\ 



]*_fj* h** 



ndichiteni kukhala Woyanjidwa 
(ndi Inu)" 

7. Adauzidwa): "E, iwe 
Zakariya! Ife Tikukuuza nkhani 
yabwino yakuti Ubereka mwana 
dzina lake Yahaya Palibe 
patsogolo pake amene Tidamutcha 
dzina longa lake." 

8. (Zakariya) adati: "Mbuye 
wanga! Ndingapeze mwana bwanji 
pomwe mkazi Wanga ndi 
nkhalamba yosabereka ndipo Ine 
ndafikanso paukulu wopyola 
muyeso?" 

9. Adati: Ndimomwemo. 
Mbuye wako wanena (Kuti), "Izi 
nzofewa kwa Ine; ndithu, 
Ndidakulenga kale pomwe iwe 
Sudali kanthu." 

10. Adati: "Mbuye wanga 
ndipatseni Chizindikiro 
(chodziwitsa kuti mkazi Wanga ali 
ndi pakati)." Adati: "Chizindikiro 
chako ndikuti sudzatha Kuyankhula 
ndi anthu mpaka masiku atatu 
Pomwe iwe uli bwinobwino." 

11. Ndipo adatuluka kuchipinda 
Chopempherera ndikuonekera kwa 
anthu ake Ndipo adawalozera 
(pomwe Sadathe kuyankhula) kuti 
lemekezani Mulungu m'mawa ndi 
madzulo. 

12. "E, iwe Yahaya! Gwira 
Buku ili Mwamphamvu (ndi 


















'pMwn&a$\£<g± 



Surat 19. Maryam Juzu 16 I 640 I ^ 1 *jJt-i 



\ H (Cy Oj^ 



mwachidwi)." Ndipo tidampatsa 
nzeru ali mwana. 

13. Ndipo uku kudali 
kuwamvera chisoni (makolo Ake) 
chochokera kwa Ife ndi 
Kumuyeretsa (mwanayo). 
Choncho adali woopa Mulungu, 

14. Komanso wochitira 
zabwino makolo ake Ndipo sadali 
wodzitukumula (kwa anthu) 
Kapena kunyoza (Mulungu). 

15. Ndipo mtendere wa 
Mulungu udali Paiye kuyambira 
tsiku lomwe Adabadwa ndi tsiku 
lomwe adamwalira, Ndi tsiku 
limene adzaukitsidwa kuimfa 
Kukhala wamoyo. 

16. Ndipo mtchule Maryam 
m'buku Hi pamene adadzipatula 
Ku anthu a kubanja lake (Ndikunka) 
kumalo ambali ya kummawa. 1 

17. Ndipo adadzitsekereza Kwa 
iwo (kuti athe kutumikira Mulungu 
Mokwanira) choncho tidatuma 
Mngelo Wathu (Gabriel) kwa iye 
Ndipo adadzifanizira kwa iye 
Monga munthu weniweni. 






^&$&'*&l$3 









M'sura iyi muli nkhani zododometsa. Yoyamba njakubadwa kwa Yahaya 
(Yohane) yemwe adabadwa kuchokera kwa nkhalamba ziwiri zotheratu; 
pomwe mwamuna adali ndi zaka 120 ndipo mkazi adali ndi zaka 98. Choncho 
kubadwa kwa Yahaya kudali kododometsa. Koma kubadwa kwa Isa (Yesu) 
ndikumene kudali kododometsa zedi poti iye anabadwa kwa namwali 
wosakwatiwa.Tero iye anamubereka popanda wamwamuna. Zonsezi 
Mulungu adafuna kuwadziwitsa anthu ndi kuwatsimikizira kuti lye ali ndi 
mphamvu zolengera munthu popanda mwamuna. 



Siirat 19. Maryam Juzu 16 



641 



n ^jA-t 



1 ^ £.j* 5j>- 






& 



U<Wi 






& 



3WjlA<JP*~+1 






18. (Maryam) adati: "Ndithu, 
ndikudzichinjirizaNdi Mulungu 
Mwini chifundo chambiri, kwa 
Iwe ngati umaopa Mulungu." 

19. (Mngelo) adati: "Ndithu, ine 
ndine Mtumiki wa mbuye wako, 
(ndadza) Kuti ndikupatse mwana 
woyera." 

20. Adati: "Ndingakhale bwanji 
ndi mwana pomwe Sadandikhudze 
mwamuna (aliyense), ndipo Ine 
sindili (mkazi) wachiwerewere?" 

21. (Mngelo) adati;"Ndi 
momwemo"Mbuye Wako akuti: 
"Zimenezi kwa Ine nzosavuta. 
Ndipo timchita kukhala 
chozizwitsa Kwa anthu ndi 
mtendere Wochokera kwa Ife. 
(Nchifukwa chake Tachita izi;) 
ndipo ichi ndi chinthu Chimene 
chidalamulidwa kale, (chichitika 
Monga momwe Mulungu 
adafunira)." 

22. Choncho adatenga pakati 
pake, Ndipo adachoka ndi pakatipo 
kunka Kumalo akutali. 1 

23. Ndipo matenda auchembere 
(atakwana), Adampititsa kuthunthu 
lamtengo wa Kanjedza (wouma 
kuti awutsamire pomubala 



1 Izi zidachitika pamene Gabriel adauzira m'thumba la chovala cha Maryam. 
Ndipo mpweya udafika mpaka m'mimba mwake. Choncho atakhala ndi pakati 
anadzipatula kwa anthu kunka kutali ali ndi pakati pamwana wakeyo kuti 
anthu angamdzudzule pokhala ndi mimba yosadziwika mwamuna wake. 



®4^fc^S&\tfs« 






Surat 19. Maryam Juzu 16 I 642 I ^ n *jJH 



> S f_y 5jj-- 



Mwanayo) adati: "Kalanga ine! 
Ndiponi Ndikadafa izi 
zisanachitike Ndikadakhala 
nditaiwalidwa, ndithu." 

24, Kenaka (Mngelo) 
adamuitana kuchokera Chapansi 
pake (kumuuza kuti): 
"Usadandaule. Ndithu, Mbuye 
wako Wakupangira kamtsinje 
pansi pako; 

25, Ndipo ligwedezere kumbali 
yako thunthu Lamtengo 
(woumawo). Zipatso zabwino 
Zakupsa zikugwera. 1 

26, Choncho udye ndi kumwa 
ndikutonthoza Diso lako, (khala 
ndi mpumulo wabwino). Ndipo 
ukaona munthu aliyense (akafunsa 
Za mwanayo), nena: "Ndithu, ine 
ndalonjeza Kwa (Mulungu) Mwini 
chifundo chambiri Kumanga kuti 
lero sindiyankhula ndi Munthu 
aliyense." 

27, Ndipo adadza naye 
(mwanayo) kwa anthu Ake 
atamnyamula. (Anthu)adati: "E, 
Iwe Maryam! Ndithu, wabwera ndi 
chinthu Chachikulu; 
(chododometsa)"; 












®V 



*»*.*-* 



1 Omasulira adati: Adamulamula kuti agwedeze thunthu lamtengo wouma kuti 
aone chizizwa chachiwiri mtengo wouma pokhala wauwisi ndikubereka 
zipatso nthawi yomweyo zakupsa. Adamuonetsanso kasupe wamadzi okoma 
yemwe anafwamphuka uku iye akuona. Ndipo iye adali kudya zipatsozo 
nkumamwera madziwo. Uku kudali kumulimbikitsa mtima kuti asade nkhawa 
pokhala ndi mwana wdpanda tate wake koma zonsezi wazichita ndi Mulungu. 



Surat 19. Maryam Juzu 16 



643 



n *>» 



^ * fs 5 jj-* 



28. "E, iwe mlongo wa 
Haaruna! Bambo wako Sadali 
munthu woipa, ngakhalenso mayi 
Wako sadali wachi were were." 1 

29. (Maryam sadawayankhe) 
koma adaloza kwa iye (Mwanayo 
kuti ayankhule naye). Ndipo iwo 
Adati: "Timuyankhula chotani 
mwana yemwe ali m'chikuta?" 

30. (Mwanayo) adanena: "Ine 
ndine kapolo wa Mulungu. 
Wandipatsa Buku ndikundichita 
Kukhala Mneneri; 

31. Ndipo wandichita kukhala 
Wodala paliponse pomwe ndili, 
Ndipo wandilamula kuswali ndi 
Kupereka Zakat pomwe ndili moyo. 

32. Ndipo wandilangiza 
kuchitira mayi Wanga zabwino, 
ndipo sadandichite Kukhala 
wodzikuza, (woipa) watsoka; 

33. Ndipo mtendere uli pa ine 
kuyambira Tsiku lomwe 
ndidabadwa ndi tsiku Limene 
ndidzamwalira, ndi tsiku limene 
Ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku 
lachiweruzo) Ndikukhala ndi moyo." 

34. Uyu ndi Isa (Yesu) mwana 
wa Maryam: (Awa ndi) mau 






mi 






&Cfi&&\&<& 



1 Katada adaati: Haaruna adali munthu wolungama kwambiri mumtundu wa 
Ana alsraeli. Adalj wotchuka kwambiri pazakulungama. Choncho Ana alsraeli 
adali kufanizira Maryam ndi Haaruna chifukwa cha kulungama kwake; sikuti 
Maryam adali mlongo wake weniweni wa Haaruna yemwe adali m'bale wa 
Musa. Pakati pa Maryam ndi Haaruna padapita zaka chikwi chimodzi. 



Surat 19. Maryam Juzu 16 



644 



n *>» 



y^f^hj-* 



owoona omwe (Akhrisitu) 
Akuwakaikira. 

35. Sikoyenera kwa Mulungu 
kudzipangira Mwana. lye 
(Mulungu) wapatukana ndi 
Zimenezi. Akafuna chinthu, 
amangonena Kwa chinthucho 
"chitika," ndipo icho Chimachitikadi. 

36. (Yesu adati:) "Ndipo ndithu, 
Mulungu ndi Mbuye wanga 
ndiponso Mbuye wanu. Choncho 
mpembedzeni; iyi njira yolunjika 
(Yokufikitsani ku mtendere.) 1 

37. Koma magulu (a Akhrisitu 
ndi Ayuda) Adapatukana pakati 
pawo; (ena adamuyesa Yesu kuti 
ndimwana wa Mulungu, ndipo Ena 
adamuyesa Mulungu weniweni 
pomwe Ayuda ankati ndi mwana 
wobadwa M' njira ya chi were were) 
choncho chilango Chaukali 
chidzatsimikizika pa amene 
Sadakhulupirire pokaonekera tsiku 
Lalikululo (kwa Mulungu). 

38. Taona kumvetsetsa kwawo 
Ndikupenyetsetsa kwawo Tsiku 
lodzatidzera, (kudzanenedwa kuti:) 
"Koma osalungama lero ali 
m'kusokera koonekera". 















1 Umu ndimomwe Yesu adanenera za ukapolo wake kwa Mulungu. lye sadali 
Mulungu kapena mwana wa Mulungu, kapena mmodzi wa atatu monga 
momwe Akhrisitu amanenera. Koma iye adali kapolo wa Mulungu ndiponso 
Mtumiki wake. Chauta adamulenga mwa mayi popanda bambo kuti akhale 
chisonyezo chosonyeza mphamvu za Mulungu zoposa. 



Surat 19. Maryam Juzu 16 645 * 1 *j^ 



n 



f-j* *jj~> 



39. Ndipo achenjeze (anthu) za 
tsiku la Madandaulo, pamene 
chiweruzo chidzagamulidwa, 
(Abwino kulowa ku munda 
wamtendere, Oipa kulowa ku 
moto); koma iwo(pano Padziko 
lapansi) ali m'kusalabadira Ndipo 
sakhulupirira. l 

40. Ndithu, Ife Tidzaitenga 
nthaka ndi Amene ali pamenepo; 
(zonse zidzakhala za Ife) Ndipo 
kwa Ife adzabwezedwa. 

41. Ndipo mtchule m'buku ili, 
Ibrahim. Ndithu, iye adali wonena 
zoona Zokhazokha, Mneneri. 

42. (Akumbutse) pamene iye 
adauza bambo wake: "E, inu 
bambo wanga! Bwanji 
mukupembedza Zomwe sizimva 
ndiponso sizipenya, ndiponso 
Zosakupindulitsani chilichonse?" 



1 Tsiku la Kiyama (chimaliziro), anthu oipa adzadandaula kwambiri. Tsiku 
limenelo kwa iwo lidzakhala tsiku lamadandaulo okhaokha, osatinso 
chinachake.M'buku la swahihi la Musilimu muli hadisi ya Abi Saidi Khuduriyi. 
lye adati: Ndithu, Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale ndi iye) adati, 
"Pamene anthu olungama adzalowa kumunda wamtendere ndipo anthu oipa 
kumoto, imfa idzadza tsiku la chimalizirolo. Idzaoneka ngati nkhosa yabwino. 
Ndipo idzaikidwa pakati pamunda wamtendere ndi moto. Tsono 
kudzanenedwa, "E, inu eni munda wamtendere! Kodi ichi 
mukuchidziwa?"Onse adzatukula makosi kuyang'ana nkuzati: "Inde iyo ndi 
imfa." Kenako kudzanenedwa: "E inu anthu akumoto kodi ichi mukuchidziwa?" 
Onse adzatukula makosi awo kuyang'ana nkuzati: "Inde iyo ndi imfa." Ndipo 
kudzalamulidwa kuti izingidwe. Kenako kudzanenedwa: "E, inu eni munda 
wamtendere! Khalani muyaya m'menemo, palibe imfanso. Ndiponso inu eni 
moto khalani muyaya mmenemo palibe imfanso. "Kenako Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) adawerenga aya (ndime) yakuti: "Achenjeze 
zatsiku lamadandaulo aakulu". 












Surat 19. Maryam Juzu 16 I 645 I \ *\ *j*-i 



H 



f j* •j>* 



43. "E, inu bambo wanga! 
Ndithu, ine Zandidzera nzeru 
(zomuzindikira Mulungu) Zomwe 
sizidakudzereni; choncho 
nditsateni. Ndikutsogolereni 
kunjira yolungama. 

44. E, bambo wanga! 
Musapembedze satana (Potsatira 
malangizo ake). Ndithu, satana 
Ngopandukira (Mulungu) Mwini 
Chifundo Chambiri. 

45. E, bambo wanga! Ndithu, 
ine ndikuopa kuti Chilango 
chingakukhudzeni chochokera 
Kwa (Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri, Ndipo potero mdzakhala 
bwenzi la satana." 

46. (Bambo wake) adati: "Kodi 
iwe ukuda Milungu yanga, E, iwe 
Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza 
milungu yanga) Ndikugenda ndi 
miyala; choncho ndichokere Kwa 
nthawi yaitali (tisaonanenso)." 

47. (Ibrahim) adati: "Mtendere 
ukhale pa inu! Ndikupempherani 
chikhululuko kwa Mbuye Wanga 
(ngakhale mwandipirikitsa). 
Ndithu, iye amandichitira chisoni 
kwambiri. 

48. "Ndipo ine ndikupatukirani 
ku zomwe Mukuzipembedzazo 
kusiya Mulungu Ndipo ndipempha 
Mbuye wanga; ndithu Sindikhala 
watsoka popempha Mbuye wanga". 









$&%&&£$&» 

$&$&£&&! 









Surat 19. Maryam Juzu 16 



647 



n *>» 



^ * f-S b** 



49. Ndipo pamene 
adawapatukira ndi zimene adali 
Kuzipembedza kusiya Mulungu, 
tidampatsa iye Isihaka, ndi 
Yakubu, ndipo aliyense wa iwo 
Tidampanga kukhala M'neneri. 

50. Ndipo tidawapatsa iwo 
chifundo Chathu, Ndi kuwayikira 
iwo kutchulidwa kwabwino, 
Kwapamwamba (pakati 
pazolengedwa). 

51. Ndipo mtchule Musa 
M'buku (ili) Ndithu, iye adali 
wosankhidwa ndi Woyeretsedwa: 
ndipo adali Mtumiki M'neneri. 

52. Ndipo tidamuitana kumbali 
yakudzanjadzanja La phiri la Turi, 
ndipo tidamuyandikitsa ndi 
Kuyankhula Nafe 
momunong'oneza. 

53. Ndipo mwachifundo Chathu 
tidampatsa (Musa) M'bale 

wake Haaruna kukhala mneneri 
(Womuthangata) 

54. Mtchulenso M'buku (ili) 
Ismaila; ndithu, Iye adali woona 
palonjezo, ndipo adali Mtumiki 
Mneneri. 

55. Adali kulamula anthu ake 
swala ndi Zakat, ndipo kwa mbuye 
wake adali Woyanjidwa. 

56. Mtchulenso M'buku (ili) 
Idirisa, Ndithu, iye adali wonena 
Zoona zokhazokha, Mneneri. 



©^c|o*e 






r^ IV <Jty S 9 



Surat 19. Maryam Juzu 16 648 ^ *i *j*-' 



S <\ f mJ A 5j^ 



57. Ndipo tidamuika malo 
Apamwamba. 

58. Iwowo ndi omwe 
adawadalitsa Mulungu, mwa 
aneneri mu ana a Adam, Ndi 
(m'mbumba ya) amene 
tidawatenga pamodzi ndi Nuhi 
(m'chombo), Ndi m'mbumba ya 
Ibrahim ndi Israeli Ndi amene 
tidawaongola ndi kuwasankha. 
Ndipo zikawerengedwa kwa iwo 
aya za (Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri, Amagwa ndi kulambira 
uku akulira. 

59. Koma pambuyo pa iwo 
padadza anthu oipa. Adasokoneza 
swala (adasiya kupemphera) 
Natsatira zilakolako zoipa; Choncho 
adzakumana ndi chilango choipa. 

60. Kupatula amene ati alape 
ndikukhulupirira Ndikuchita 
zabwino; iwowo adzalowa ku 
Munda wa mtendere ndipo 
sadzachitidwa Chinyengo pa 
chilichonse. 

61. Munda wamuyaya umene 
(Mulungu) Wachifundo chambiri 
Walonjeza akapolo Ake Mobisika 
ndithu lonjezo Lake ndilakudza. 

62. Sakamva m'menemo mawu 
achibwana, Koma mawu 
amtendere; ndipo akapeza Riziki 
(chakudya) lawo m'menemo 
M'mawa ndi madzulo. 









< "*&'. 









Surat 19. Maryam Juzu 16 649 > 1 pjk- 



\ * f.jA *jj~> 



63. Umenewo ndiwo munda 
wamtendere umene Tikawapatsa 
ena mwa akapolo athu omwe Adali 
oopa Mulungu. 

64. (Mtumiki adapempha 
Gabriel kuti akhale Akum'bwerera 
pafupipafupi. Ndipo Gabriel 
adamuuza kuti): "Ndipo 
sitimatsika Koma mwalamulo la 
Mbuye wako. Zapatsogolo pathu 
ndi zapambuyo pathu Ndi zapakati 
pazimenezi zonse Nzake 
(akuzidziwa bwinobwino). Ndipo 
Mbuye wako sali Woiwala. 

65. Mbuye wa thambo ndi 
nthaka ndi zapakati Paizo: 
Choncho mpembedze iye basi. 
Ndipo pitiriza ndikupirira 
Popembedza Iye. Kodi 
ukumudziwa (Wina) yemwe ali 
Wofanana naye (Mulungu)?" 

66. Ndipo munthu (wokanira) 
amanena: "Kodi ndikadzafa 
nzoonadi kuti Ndidzatulutsidwa 
(m'manda) Nkukhala wamoyo?." 

67. Kodi munthu sakumbukira 
kuti Tidamulenga kale pomwe 
sadali Chilichonse? 

68. Choncho ndikulumbira 
Mbuye wako ndithu, 
Tidzawasonkhanitsa iwo pamodzi 
ndi Asatana; ndipo tidzawafikitsa 
m'mphepete Mwa Jahannama uku 
atagwada. 









(±^v^fy?QC^\ $&} 









Surat 19. Maryam Juzu 16 



650 



n *>•» 



) * fljA 5j^ 



69. Kenako, m'gulu lililonse 
tidzachotsamo Yemwe adali 
wopyola malire polakwira 
(Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri. 

70. Ndipo Ife tikuwazindikira 
kwambiri Amene ali oyenera 
kulowa M'moto. 

71. Ndipo palibe aliyense mwa 
inu Koma adzaifika 
(Jahannamayo). Ndithu Hi ndi 
lamulo la Mbuye wako lomwe 
Lidalamulidwa kale. 

72. Ndipo kenako 
tidzawapulumutsa amene Ankaopa 
Mulungu ndipo osalungama 
Tidzawasiya m'menemo atagwada. 

73. Ndipo aya Zathu zomveka 
bwino zikawerengedwa kwa iwo, 
omwe sadakhulupirire Amanena 
kwa omwe akhulupirira: "Ndi gulu 
liti pamagulu awiri awa, (Lanu ndi 
lathu) lomwe lili ndi pokhala 
Pabwino ndikukhalanso ndi anthu 
Olemekezeka?" 

74. Ndipo mibadwo yambiri 
tidaiononga Patsogolo pawo, 
Yomwe idali ndi ziwiya Zabwino 
ndi maonekedwe abwino. 

75. Nena: "Amene ali 
mkusokera, (Mulungu) Mwini 
chifundo chambiri amuonjezera 
Nthawi yamoyo kufikira azione 









^i^teawffigj 






Surat 19. Maryam Juzu 16 I 651 I \ *\ t$?\ 



\ \ fijA S j>*> 



zomwe Akulonjezedwa- kapena 
chilango Kapena kudza nthawi (ya 
Kiyama) Pamenepo ndipomwe 
adzadziwa kuti Ndani mwini 
kukhala pamalo poipa, ndi Mwini 
wa ankhondo ofooka (Iwo kapena 
Asilamu)?" 

76. Ndipo Mulungu 
amawaonjezera chiongoko Amene 
aongoka. Ndipo zochita zabwino 
Zonkerankera (mpaka tsiku 
Lachimaliziro), ndizo zili zabwino 
Kwa Mbuye wako monga mphoto, 
Ndiponso ndiko kobwerera 
kwabwino, (Osati zamdziko Zomwe 
anthu osalungama akunyadira). 

77. Kodi wamuona yemwe 
watsutsa aya Zathu Ndikunena 
kuti: "Ndithu, Ndidzapatsidwa 
chuma ndi ana (pa tsiku 
Lachimaliziro monga momwe 
andipatsira Pano padziko?)" 

78. Kodi adapenya zamseri, 
kapena adalandira Lonjezo kwa 
Mulungu mwini chifimdo Chambiri 
(kotero kuti ali ndi chikhulupiriro 
Pazimene akunenazo)?. 

79. Sichoncho,ndithu tikulemba 
zonse zomwe Akunena, ndipo 
tidzamuonjezera nyengo Yotalika 
m' chilango. 

80. Ndipo tidzamlowa mmalo 
zimene akunenazi, (Chuma ndi 
anawo), nadzatidzera Ali 





















0l, 



Surat 19. Mary am Juzu 16 



652 



n *>i 



^ * fljA Sj^rf 



yekhayekha (wopanda chuma ndi 
Zonse zomwe ankanyadira). 

81. Eti adzipangira milungu ina 
m'malo Mwa Mulungu kuti 
milunguyo iwapatse Mphamvu 
(ndi ulemerero). 

82. Iyayi! Idzawakanira 
Mapemphero awo Ndikuwaukira. 

83. Kodi suona kuti Ife 
timawatuma Asatana kwa 
osakhulupirira ndipo 
Akuwakhwirizira kwambiri 
(kuchita Zoipa)? 

84. Choncho, usawachitire 
changu (kuti Alangidwe tsopano), 
ndithu, Ife Tikuwawerengera 
chiwerengero (cha Masiku awo; 
masiku akakwana, Tiwalanga.) 

85. (Kumbukira iwe Mtumiki) 
tsiku lomwe Tidzawasonkhanitsa 
oopa (Mulungu) Kunka nawo 
kumunda wa Mwini chifundo 
Chambiri ali m'magulumagulu 
monga Nthumwi zake (kuti 
apatsidwe ulemu.) 

86. Ndipo oipa tidzawakusa 
kunka nawo Ku moto uku ali ndi 
ludzu lalikulu. (Monga momwe 
ziweto zimathamangira Kupita 
kumadzi zikakhala ndi ludzu 
Lalikulu). 

87. Sazakhala ndi mphamvu 
yoombolera (ena) Koma kupatula 



;ffli©^S&!332S 



2Jb 



^ 









txpmt&s& 



^^>jia«ss 



A\*' '1"" H| '* »f\L*X€ 



<&ffi^X&&&$ 



Surat 19. Maryam Juzu 16 



653 



n *>-i 



)% 



f-j> hf 



omwe adagwiritsa lonjezo la 
(Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri. 

88. Ndipo (osakhulupirira 
omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu) 
akuti "(Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri Wadzipangira Mwana!" 

89. Ndithu, mwadza ndi chinthu 
choipitsitsa Kwambiri (pazimene 
mukunenazi). 

90. Thambo layandikira 
Kusweka ndi mawuwo, Ndipo 
nthaka kuphwasuka, ndipo mapiri 
Kugwa ndikudukaduka. 

91. Chifukwa chakumunamizira 
(Mulungu) Mwini chifundo 
chambiri kuti ali ndi Mwana. 

92. Ndipo nkosayenera kwa 
(Mulungu) Mwini Chifundo 
chambiri kudzipangira mwana. 

93. Palibe aliyense yemwe ali 
kumwamba ndi Pansi koma 
adzadza kwa (Mulungu) Mwini 
Chifundo chambiri ali kapolo 
(Wake). 

94. Ndithu (Mulungu) 
wawadziwa mokwanira Ndipo 
adzawawerenga aliyense 
Payekhapayekha. 

95. Ndipo, aliyense wa iwo 
adzadza kwa lye (Mulungu) ali 
payekhapayekha 



s«^i 



w&&@&& 



M^.'SLs? 



*< 9 .C'?> '9titff> "W& 






Surat 19. Maryam Juzu 16 



654 



n ^jA-i 



^ ^ f.y 6j** 



96. Ndithu amene akhulupirira 
Ndi kumachita zabwino, 
(Mulungu) Mwini chifundo 
Chambiri adzaika chikondi Pakati 
pawo. 

97. Ndithu, taifewetsa (Qur'an) 
M'chiyankhulo chako kuti ndi iyo 
Uwawuze nkhani zabwino oopa 
Mulungu ndipo ndi iyo 
uwachenjeze Anthu amakani. 

98. Kodi ndi mibadwo ingati 
tidaiononga Patsogolo pawo? Kodi 
ukumuona Mmodzi wa iwo, 
kapena ukumva Mgugu wawo? 













Surat 20. Ta-Ha Juzu 16 655 ^ *j*-» t • & i^ 




Sura iyi idavumbulutsidwa ku Makka kupatula aya ziwiri 
zomwe ndi aya ya 130 ndi 131. Sura iyi yayamba ndi malembo 
awiri omwe akusonyeza kuti Qur'an njachidule ndi yomveka. 
Ndipo pambuyo pa malembo awiri, Surayi yafotokoza za 
Ulemerero wa Qur'an ndi kutukuka kwa Yemwe adaivumbulutsa, 
yemwe ndi Mulungu Woyera, Mwini thambo ndi nthaka; 
Wodziwa zobisika zonse. 

Surayi yafotokozanso nkhani ya Musa ndi Farawo ndi 
momwe utumiki wa Musa udayambira. Ndikutinso iye (Musa) 
adapempha Mulungu kuti asankhe Haaruna kukhala mthandizi 
wake. Ndipo yafotokozanso momwe Musa, Haaruna ndi Farawo 
adakumanirana pomwe adali kuopa kukumana naye chifukwa 
chakuipa mtima kwake ndi nkhanza zake. Ndipo Mulungu 
wafotokozanso momwe Musa (A.S) adaleredwera. 

M' surayi mulinso za momwe Musa ndi Farawo 
ankabwezerana mawu ndi pakati pa Musa ndi amatsenga, ndi 
mantha a Musa ngati amatsenga atapambana. Ndipo mulinso 
mawu oti pomwe Musa adaponya ndodo yake, idameza zingwe 
za amatsenga zomwe zimaoneka ngati njoka. Ndipo 
yafotokonzanso mathero a zochitachita za amatsenga, kuti iwo 
adakhulupirira ndipo Farawo adawalanga chifukwa cha 
kumkhulupirira Musa. 

Surayi yafotokozanso zakupulumuka kwa Musa ndi ana a 
Isiraeli kuchiwembu cha Farawo ndi momwe Farawo 
adamizidwira m'madzi. Izi zidachitika pamene Musa 
adamenyetsa ndodo panyanja ndipo madzi adagawikana, iwo 
nkulowapo. Ndipo naye Farawo adatsatira. 

Surayi yatinso pamene Musa adaoloka, adaitanidwa kuphiri 
ndi Mulungu kuti akanene naye. Ndipo iye atapita kuphiri, 
Samiriyu adawasokoneza ana a Israeli powalangiza 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



656 



n *>i 



Y * <& Sjj-*» 



zakupembedza mwana wa ng'ombe wopangidwa ndi golide. 
Pazomwe zidachitikazi, Musa adakwiya kwambiri kotero kuti 

adagwira mutu wa mbale wake Haaruna ndi kumaukoka. 
Komanso surayi yafotokoza za chilango chomwe chidampeza 
Samiriyu. Ndipo Mulungu wasonyeza phunziro lomwe lili 
m'nkhani ya Musa ndi aneneri ena. Ndipo kumalekezero kwa 
surayi kuli malangizo a kupirira, kupewa makhalidwe oipa 
ndikufunika kwa swala. 

Kothera kwenikweni Surayi yalongosola za chilango chomwe 
osakhulupirira adzalandira, ndi mtendere womwe anthu abwino 
adzapeza. 




Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



657 1 1 *>» 



Y • *k 5jj-*» 



Swraf 7a-Jfa AST 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisonl 

\.Ta-Ha x 

2. Sitidakuvumbulutsire iwe 
Qur'an kuti Uvutike nayo, 

3. Koma kuti ikhale ulaliki ndi 
chikumbutso Kwa yemwe akuopa 
(ndikudzichepetsa Kwa Mulungu). 

4. Chovumbulitsidwa 
chochokera kwa Yemwe adalenga 
nthaka ndi thambo Lotukuka 
kumwamba. 

5. (lye ndi Mulungu),Wa 
chifundo Chambiri; pampando 
wachifumu Adakhazikika, 
(kukhazikika Koyenerana ndi 
ulemerero Wake Kopanda 
kukufanizira ndi kukhazikika Kwa 
chilichonse; pakuti lye salingana 
Ndi chilichonse pachikhalidwe ndi 
Mbiri zake). 

6. Zonse zakumwamba ndi 
zapansi ndi Zapakati pake ndi 
zapansi Pa nthaka, nza lye. 




o^l^fcfcW- 



-^ 









Mulungu wapamwamba wayamba Sura iyi ndi malembo awa awiri 
potchalenja omwe akutsutsa zoti Qur'an idachokera kwa Mulungu, kuti 
atalemba yawo Qur'an yomwe malembo ake omwewa omwe iwo akuwadziwa 
bwino ndipo amawayankhula. 

Koma alephera kutalitali kulemba Buku ndi nzeru zawo monga ili. Ndipo 
kulephera kwawo kulemba Buku longa ili, ndiumboni kuti Bukuli lidachokera 
kwa Mulungu. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



658 



vn *>» 



t% & 



•j>* 



7. Ndipo ngati ulankhula 
mokweza mawu, (Iwe munthu), 
ndithu, lye akudziwa Zobisika ndi 
zobisika kwambiri Kwambiri 
(mwazibisa mumtima mwanu). 1 

8. Mulungu! Palibe 
wopembedzedwa Mwachoonadi 
koma lye. lye ali Ndi maina 
abwino (ndi mbiri zabwinonso). 

9. Ndipo kodi yakufika nkhani 
ya Musa? (Yomwe njododometsa)? 2 

10. Pamene adaona moto 
adauza banja lake: "Yembekezani 
(pano); ndithu, ndaona moto; 
Mwina ndingakakutengereni 
chikuni chamoto (Kuti muothe), 
kapena ndikapeza Ondiongolera 
njira pamotopo. 

11. Koma pamene adaudzera 
motowo Anaitanidwa (kuti), "E, 
iwe Musa! 

12. Ndithu, ine ndine mbuye 
wako! Vula Nsapato zakozo; 






*u&&Z£&&yi 



^ 






V;j&yy%& 



,OV«38e03?tt««3B«S3l 



1 M'ndime iyi Chauta akuuza munthu kuti lye akudziwa zonse zimene munthu 
amayankhula mokweza mawu ndi zimene munthu amayankhula ndi anzake 
mobisa, ngakhalenso zomwe mtima wake umamnong'oneza. 

2 fbun Abbas adati: "Izi zidali choncho Mussa pamene adakwaniritsa 
chipangano cha nthawi imene adapangana ndi m'neneri Shuaibu chakuti 
amuwetere mbuzi kwa zaka 8 kapena 10, adachoka ulendo kubwerera kwawo 
ku tguputo pamodzi ndi banja lake; ndipo adasokera njira. Udali usiku 
wamdima wozizira. Adayesa kupekesa moto kuti awothe koma adalephera. 
Ndipo ali choncho, adangoona moto chapatali kumbali yakumanja kwa njira. 
Pamene adauona adauganizira kuti ndi moto weniweni, pomwe udali moto 
woyera wakuunika kwa Mulungu. Udali kuyaka mumtengo wamasamba 
obiriwira. Ndipo adangomva Mbuye wake akumuitana: "E, iwe Musa! Ine 
ndine Mbuye wako. Ndikukuyankhula; vula nsapato zako." 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



659 



U *>i 



Y * de <*JJ-** 



ndithu, iwe uli Pa chigwa 
chopatulika, chotchedwa Tuwa. 

13. Ndipo Ine ndakusankha 
(kuti ukhale Mtumiki); choncho 
mvera zonse Zomwe 
zikuvumbulutsidwa (kwa iwe). 

14. Ndithu, Ine ndine Mulungu 
palibe Wopembedzedwa 
mwachoonadi koma Ine; choncho 
ndipembeze, pemphera Swala 
moyenera pondikumbukira. 

15. Ndithu, nthawi ya tsiku 
lachimaliziro Idza; (choncho 
Ikonzekere ndi ntchito Zabwino); 
ndikuibisa dala (Kwa anthu) kuti 
mzimu Uliwonse udzalipidwe 
zimeneudachita. 1 

16. Ndipo asakutsekereze 
(kukhulupirira) Zimenezo yemwe 
saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo 
akungotsata Zilakolako za mtima 
wake; kuopakuti 
Ungadzaonongeke". 

17. "Kodi nchiyani icho chili 
kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe 
Musa?" 












«&$&S$$& 



1 Womasulira Qur'an adati cholinga chakubisa kudza kwa tsiku la chimaliziro, 
ndi nthawi ya imfa ya munthu ndikuti Mulungu wapamwambamwamba 
adalamula kuti sangavomereze kulapa tsiku la chimaliziro litadza, ndi nthawi 
ya imfa itamufikira munthu. Anthu akadadziwa nthawi yeniyeni ya chimaliziro 
ndi nthawi yakudza kwa imfa yawo, akadakhala akuchita zinthu zoyipa 
naakhala ndi chiyembekezero choti adzalapa nthawi ikayandikira, 
nadzapulumuka kuchilango cha Mulungu. Koma Mulungu anabisa zimenezo 
kuti anthu akhale tcheru nthawi zonse ndikukhala okonzekera za imfa ndi za 
tsiku la chimaliziro kuti zingawadzere modzidzimutsa. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



660 



>n *jA-» 



Y * 4^ djj-* 



18. (Musa) adati: "Iyi ndi ndodo 
yanga, Ndimaitsamira (poyenda) 
ndi kuphopholera Masamba 
ambuzi zanga; ndiponso 
(M'ndodomo) muli zina 
zondithandiza." 1 

19. (Mulungu) adati: "Iponye 
iwe Musa!" 

20. Ndipo adaiponya; pompo 
idasanduka Njoka yoyenda 
mothamanga. 

21. (Mulungu) adati: "Igwire, 
usaope. Tiibwezera m'chikhalidwe 
chake Choyamba. 

22. Ndipo lipane dzanja lako 
m'khwapa mwako Lituluka lili 
loyera (ngati kuwala Kwadzuwa 
ndi mwezi). Osati mwamatenda, 
(Ichi chikhala) chozizwitsa china, 3 

23. Kuti tikusonyeze zina mwa 
zozizwitsa zathu, Zazikuluzikulu. 

24. Pita kwa Farawo, ndithu, 
iye wapyola Malire." 












1 Womasulira adati yankho lakuti "Iyi ndi ndodo yanga" lidati yankho lokwana. 
Koma iye adaonjezera payankho mawu ena amene sadamufunse chifukwa 
chakuti pomwe adalipo padali pamalo poyenera kutambasuia mawu pakuti 
Mulungu ndiye adali kuyankhula naye popanda mkhalapakati. Uku kudali kuti 
amve kukoma koyankhulana ndi Mulungu. Pajatu mawu a wokondedwa 
amatonthoza moyo ndipo amachotsa kutopa kwa mtundu uliwonse. 

2 Ibun Abbas adati ndodoyi idasanduka chinjoka chachimuna chomwe chidali 
kumeza miyala ndi mitengo. Pamene Musa adachiona chikumeza chilichonse 
adachiopa. Nkhaniyi ikupezeka m'buku la kurutubi, volume 11, tsamba la 190. 

3 Ibun Kathiri adati Musa ankati akalilowetsa dzanjalo mkhwapa mwake 
kenako nkulitulutsa, limatuluka tili kung'anima ngati chipande chamwezi 
popanda chonyansa chilichonse. Ichi chidali china mwa zozizwitsa zake. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



661 



>n *yk\ 



r • A 



d j>- 



25. (Musa) adati: "E, Mbuye 
wanga! Nditsakulireni chifuwa 
changa; 

26. Ndi kundifewetsera ntchito 
yangayi (Imene mwandipatsa kuti 
uthengawu Ndikaufalitse m'njira 
yoyenera); 

27. Ndipo masulani mfundo 
yomwe Hi kulirime kwanga, 
(ndimasulireni Kumangika kwa 
lirime langa kuti Mawu anga 
akakhale opanda chibwibwi). 1 

28. Kuti (anthu) akamvetse 
mawu anga. 

29. Ndipo ndipatseni mthandizi 
Wochokera kubanja langa, 

30. M'bale wanga Haaruna 
(Kuti akhale nduna yanga); 

31. Limbitsani nyonga zanga 
ndi iye, 

32. Ndipo mphatikeni kuntchito 
Yangayi, 

33. Kuti tikulemekezeni 
kwambiri. 



®<^a#^$ 



?>&\ ■>«'.' 



W\\'\>l':.'il Viiir 



twd^soSs-O^-li 



©'l't£££ 






Musa adali wachibwibwi koma chibwibwi chake sichinali chachibadwa. 
Kuyamba kwa chibwibwi chake kudali motere: Kumayambiriro amoyo wake 
adali kukhala m'nyumba ya Farawo. Ndipo nthawi ina Farawo adamuika 
pamiyendo yake iye ali mwana. Musa adakoka ndevu za Farawo ndi dzanja 
lake. Ndipo Farawo adakwiya natsimikiza zomupha. Ndipo Asiya, mkazi wake, 
adati kwa iye."lyeyu sazindikira. Ndipo ndikusonyeza zimenezo kuti 
udziwe.Yandikitsani kwa iye makala awiri ndi ngale ziwiri. Ngati atola ngalezo 
ndiye kuti akuzindikira. Koma akatola khala lamoto, apo uzindikira kuti ameneyu 
sazindikira kanthu. Choncho Farawo adamuyandikizira zonsezo ndipo iye 
adatola khala lamoto nkuliponya mkamwa mwake. Potero palirime lake padali 
kachipsera. Nkhaniyi ikupezeka m'buku la Tabariyi, volume 16 tsamba 159. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



662 



n *>» 



Y * Ae °JJ~ 1 ' 



34. Ndi kukutamandani 
kwabasi. 

35. Ndithu inu (nthawi zonse) 
mumationa (Ndi kutisunga)." 

36. (Mulungu) adati: "Ndithu 
wapatsidwa Zomwe wapempha, E, 
iwe Musa 

37. Ndipo ndithu, tidakuchitira 
ubwino Nthawi ina (popanda iwe 
kutipempha), 

38. Pamena mayi wako 
tidamuzindikiritsa Zimene 
tidamzindikiritsa (kuti azichite). 

39. (Kuti): "Mponye 
(mwanayo) m'bokosi Ndipo ponya 
bokosilo mu m'tsinje; Ndipo 
m'tsinje umponya m'mbali kuti 
Amtenge mdani wanga ndi mdani 
wake (Ndi kuti aleredwe 
mwaubwino ndi Farawo); ndipo 
ndidaika kukondeka Pa iwe 
kochokera kwa Ine (kuti ukhale 
Wokondedwa ndi anthu onse) 
ndikuti Uleredwe 
moyang'aniridwa ndi Ine". 

40. (Kumbuka) pomwe mlongo 
wako Ankayenda (kunka kubanja 
la Farawo) Ndipo adati: "Kodi 
ndikulondolereni Munthu amene 
angathe kumlera?" Ndipo 
Tidakubwezera kwa mayi wako 
kuti maso Ake atonthole, ndipo 
asadandaule. Ndipo Kenaka 



®mzm 






® 



<>j&^3i&»i 



<3i£a& S *?& d&s& ti 






Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



663 



n *>» 



Y * aIp *jj~* 



udapha munthu (mwangozi), ndipo 
Tidakupulumutsa kumadandaulo; 
Tidakuyesa ndi mayeso ambiri. 
Udakhala zaka zambiri ndi anthu a 
ku Madiyani. Kenaka wabwera 
(apa) monga Mwachikonzero, ee, 
Iwe Musa! l 

41. Ndipo ndakusankha ndekha 
(kuti ukhale Mtumiki Wanga). 

42. Pita iwe ndi mbale wako ndi 
Zozizwitsa zanga, ndipo musatope 
(Musasiye) kundikumbukira. 

43. Pitani kwa Farawo, ndithu, 
iye Wapyola malire. 

44. Kamuuzeni mawu ofewa 
mwina Akalingalira (uthengawo) 
kapena Akaopa". 

45. (Iwo) adati: "Mbuye wathu 
ndithu, Ife tikuopa kuti 
angatimbwandire kapena 
Kutipyolera malire (tisananene 
Kanthu)". 



W--**)* 



«^sig£aj 



^aftaJKa^i 



ty%&&$& 



] >W& r * 



'#$$$%% 



l/Jfi 






1 Omasulira adati: Pamene adamtoia Musa akubanja la Farawo sadali 
kuyamwa bele lamkazi aliyense, amakana, chifukwa Mulungu adamuletsa 
kuyamwa mawere aakazi ena oyamwitsa. Ndipo mayi wake adali ndi 
madandaulo ndi chisoni atamponya mumtsinje, ndipo adamulamula mlongo 
wake kunka nafufuza zamwanayo. Pamene adafika kunyumba ya Farawo, 
adamuona. Adati: "Kodi ndikulondolereni mkazi wokhulupirika, waulemu kuti 
azikuyamwitsirani mwanayo?". Ndipo iwo adati pita kamtenge. Choncho 
adadza ndi mayi wa Musa. Pamene adatulutsa bere lake, Musa adayamwa. 
Choncho mkazi wa Farawo adasangalala kwabasi namuuza make Musa: 
"Dzikhala pamodzi nane kunyumba yachifumu". lye adati: "Sindingathe kusiya 
nyumba yanga ndi ana anga. Koma ndimtenga ndipo ndikhala ndikudza naye 
nthawi iliyonse ukamufuna." Mkazi wa Farawo adavomereza ndi kumchitira 
zaufulu mayiyo. Hi ndilo tanthauzo la mawu a Mulungu akuti, "Tidakubwezera 
kwa mayi wako kuti diso lake litonthole, asadandaule". 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



664 



n *>i 



y * <& 5jj-«» 



46. (Mulungu) adati: 
"Musaope.Ndithu Ine ndili nanu 
pamodzi. Ndikumva, Ndiponso 
ndikuona". 

47. Choncho mpitireni, 
ndikumuuza (kuti): "Ndithu, ife 
ndife atumiki a Mbuye wako. 
Asiye ana a Israeli achoke Ndi ife, 
ndipo usawazunze; ndithu, 
Takudzera ndi chozizwitsa 
chochokera Kwa Mbuye wako 
(chomwe ndi mboni Yathu 
pazomwe tikukuuzazi), ndipo 
Mtendere ukhala pa yemwe aatsate 
Chiwongoko 

48. Ndithu, zavumbulitsidwa 
kwa ife kuti Chilango chiwapeza 
amene akutsutsa (Zimenezi) 
ndikuzitembenukira Kumbali." 

49. (Farawo) adati: "Kodi 
Mbuye wanu Ndani, iwe Musa?". 

50. (Musa) adati: "Mbuye 
wathu ndi yemwe Adapatsa 
chinthu chilichonse Chilengedwe 
chake, kenako Adachiongolera 
(kutsata chimene Chikulingana ndi 
chilengedwe chake)." 

51. (Farawo) adati: "Nanga 
mibadwo yakale Hi bwanji, (imene 
idapita iwe Usadadze?)". 

52. (Musa) adati: "Kudziwa 
kwa zimenezo Nkwa Mbuye 
wanga, m'kaundula (Wake 



%% piQS^a^GN; 












©ja^ap* 



t^tfx&y&az 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



665 



n *>i 



Y • & ^jj**' 



Momwe mwasonkhanitsidwa 
Chilichonse), Mbuye wanga 
sasokera, Ndipo saiwala. 

53. Yemwe adakupangirani 
nthaka monga Choyala, ndipo 
m'menemo adakuikirani Njira 
ndikutsitsa madzi kuchokera 
Kumwamba". Ndipo kupyolera 
m'madziwo Tidameretsa mmera 
Wosiyanasiyana. 

54. Idyani ndikudyetsa ziweto 
zanu. Ndithu, m'zimenezo muli 
zisonyezo Kwa eni nzeru. 

55. Kuchokera (m'nthaka) umu 
tidakulengani, Ndipo momwemo 
tidzakubwezani, ndipo Kuchokera 
m'menemo tidzakutulutsani 
Nthawi ina (muli moyo). 

56. Ndipo, ndithu, tidamuonetsa 
(Farawo) Zozizwitsa zathu zonse, 
koma adatsutsa Ndipo adakana. 

57. Adati: "Kodi watidzera kuti 
utitulutse M'dziko lathu, ndi 
matsenga ako,e, iwe Musa! 

58. Choncho nafe 
tikubweretsera matsenga Onga 
amenewo! Choncho ika lonjezo 
(La msonkhano) pakati pathu ndi 
iwe; Lonjezo lomwe tisaliswe ife 
ndi iwe, (Tidzakumane) pamalo 
poyenera." 

59. (Musa) adati: "Lonjezo lanu 
likhale Pa tsiku lodzikongoletsa 


















Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



666 



11 *>■» 



Y » & °j> - ' 



(tsiku la Chikondwerero), ndipo 
anthu Adzasonkhanitsidwe 

m'mawa". 

60. Ndipo Farawo adabwerera 
ndikusonkhanitsa Matsenga ake, 
ndipo kenako adabwera (Ndi 
amatsenga ake pa tsiku la 
chipanganolo). 

61. Musa adawauza: "Tsoka 
kwa inu! Musampekere bodza 
Mulungu, kuopera kuti 
Angakuphwasuleni ndi chilango. 
Ndipo, Ndithu wataika amene 
akupeka bodza." 

62. Choncho (amatsengawo) 
adakangana pakati Pawo pazinthu 
zawo ndipo adakambirana 
Mwachinsinsi. 

63. (Iwo) adati 
(mkunong'onezana Kwawo): 
"Ndithu, anthu awiriwa Ndi 
amatsenga; kupyolera mmatsenga 
awo Akufuna kukutulutsani 
m'dziko Mwanu, ndikuchotsa 
chikhalidwe Chanu chomwe chili 
chabwino. 

64. Choncho sonkhanitsani 
matsenga anu (Onse), kenako 
mudze (kwa iwo) Mutandanda 
pamzere; ndithu lero, Apambana 
amene akhale wapamwamba." 



* A» * 



®(pj.^ 









%&\&s&$ym& 









1 Ibun Abbas adati: Amatsenga adali okwana 72. Ndipo wamatsenga aliyense 
adagwirizira m'manja mwake chingwe ndi ndodo. Izi zidalembedwa m'buku la 
Tabarivi. Volumel 1 . tsamba 214. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



667 



U ij*r\ 



T « *J? Sjj-*' 



65. (Iwo) adati: "E, iwe Musa! 
Kodi ukhala Ndiwe woyamba 
kuponya (Matsenga ako), kapena 
tikhala oyamba Ndife kuponya?" 

66. (Musa) adati: "Koma inu 
Ndinu muponye!" (Choncho 
adaponya Matsengawo). 
Mwadzidzidzi zingwe Zawo ndi 
ndodo zawo zamatsenga awo, 
Zimaoneka pamaso pake (Musa) 
kuti Zikuyenda mothamanga. 

67. Ndipo Musa adadzazidwa 
ndi mantha Mumtima mwake. 

68. Tidati: "Usaope, (zomwe 
ukuzionazi); Ndithu, iwe ukhala 
wopambana. 

69. Ndipo ponya chimene chili 
kudzanja Lako ladzanjadzanja 
(ndodo); chimeza zomwe Apanga; 
ndithu, iwo apanga matsenga a 
mfiti Ndipo mfiti siingapambane 
Paliponse pamene yadza". 1 

70. Choncho amatsenga adagwa 
Molambira uku akuti: 
"Tamkhulupirira Mbuye wa 
Haaruna ndi Musa." 









»r\i'^i\\Z\*':' l'"«\\'-X'. 






Ibun Kathiri adati: Pamene Musa adaponya ndodo idasanduka chinjoka 
chachikulu chokhala ndi miyendo ndi khosi ndi mutu ndi mano. Chidayamba 
kutsatira zingwezo ndi ndodozo mpaka chidameza zonsezo uku anthu akuona 
masomphenya masana. Amatsenga ataona zimenezo, adazindikira 
mwachitsimikizo kuti kusanduka kwa ndodoyo kukhala chinjoka sikudali 
kwaufiti kapena matsenga. Koma chidali choonadi chopanda chipeneko. 
Ndipo pamenepo onse adagwa ndi kulambira Mulungu. Tero chizizwa cha 
Mulungu chidatsimikizika. Koma zopanda pake zidapita pachabe. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



668 



n *>■» 



Y% & 



3j^ 



71. (Farawo) adanena: "Ha! 
Mwamkhulupirira 
ndisadakupatseni Chilolezo? 
Ndithu, iye ndi mkulu Wanu 
amene adakuphunzitsani 
matsenga! Choncho ndikudulani 
manja anu ndi Miyendo yanu, 
mosemphanitsa: (Dzanja 
lakudzanjadzanja ndi mwendo 
Wakumanzere. Pomwe wina, 
mkono Wakumanzere ndi mwendo 
Wakudzanjadzanja), ndipo kenako 
Ndikupachikani pamathunthu 
Amitengo ya kanjeza; ndithu, 
Mudziwa (panthawiyo) kuti ndani 
Mwa ife, (ine kapena Mulungu wa 
Musa),wachilango chaukali ndi 
Chopitirira." 1 

72. (Amatsenga) adati: 
"Sitisankha iwe kusiya Zomwe 
zatidzera; zisonyezo Zachoonadi 
zoonekera poyera! Ndipo 
tikumlumbirira Yemwe adatilenga, 
(Sitikusankha iwe), chita zomwe 
Ufuna kuchita; ndithu, iwe utha 
Kupititsa chiweruzo chokhudzana 
Ndi moyo uno wapansi, basi. 

73. Ndithu, takhulupirira 
Mbuye wathu Kuti atikhululukire 
zolakwa zathu Ndimatsenga 
amene watikakamiza (Kuchita); 
ndipo Mulungu ndi Yemwe Ali 












Imam Kurutubi adati: Ndithudi Farawo pa mawu akewa adalinga kuti 
asokoneze anthu kuti asatsatire amatsengawo kuopera kuti angakhulupirire 
monga iwo adakhulupirira. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



669 



n tj*r\ 



y ♦ *y *j>^ 



Wabwino ndi Wamuyaya (osati 
iwe)." 

74. Ndithu, amene adzadze kwa 
Mbuye Wake uku ali wamachimo, 
adzapeza Moto wa Jahannama; 
sadzafa M'menemo, ndipo 
sadzakhalanso Ndi moyo wabwino. 

75. Koma amene adzamdzera 
uku ali Msilamu, Yemwe adachita 
ntchito zabwino, iwo Ndi amene 
adzapeze ulemerero 
Wapamwamba, 

76. Minda yamuyaya, yomwe 
pansi pake ndi Patsogolo pake 
pakuyenda mitsinje. Adzakhala 
mmenemo muyaya. Ndipo 
Zimenezo ndi mphoto za yemwe 
Wadziyeretsa. 

77. Ndipo ndithu, Musa 
tidamtumizira Chivumbulutso, 
(tidamzindikiritsa kuti): "Yenda 
usiku ndi akapolo anga (kutuluka 
M'dziko la Iguputo,) ndipo 
ukawapangire Panyanja njira 
youma, ndipo usaope Kukupeza 
adani ndiponso usaope (kumira)." 

78. Choncho Farawo pamodzi 
ndi ankhondo ake, Adawatsata, 
ndipo m'nyanjamo 
Chidawaphimba chimene 
chidawaphimba. 

79. Ndipo Farawo 
adawasokeretsa anthu ake, Ndipo 
sadawaongolere. 












^I'.iV.rt 



%foj^j &j<afy>&$j 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



670 



n *>» 



t • & ^jj-*' 



80. E, inu ana a Israeli! Ndithu, 
Tidakupulumutsani kwa mdani 
wanu, ndipo Tidakulonjezani (kuti 
mudze) mbali Yakudzanjadzanja 
ya phiri (kuti Tikupatseni 
malamulo ndi zina), ndipo 
Tidakutsitsirani Manna ndi 
Saluwa. 

81. Idyani zinthu zabwino 
zomwe Takupatsani, ndipo 
musapyole malire Pazimenezo kuti 
mkwiyo wanga Usakutsikireni; 
ndipo amene mkwiyo Wanga 
wamtsikira, ndiye kuti Ameneyo 
waonongeka. 

82. Ndipo ndithu, Ine ndi 
Wokhululuka kwambiri Kwa 
amene walapa ndi kukhulupirira 
Ndikuchita ntchito zabwino, 
kenako Ndikutsata chiongoko 
mwaubwino. 

83. "Nchiyani chakufulumizitsa 
(kudza Kuno) kusiya anthu ako, 
ee, iwe Musa?" 1 

84. Adati: "Iwo ali pambuyo 
panga akunditsata. Ndachita 
changu kudza kwa Inu, Mbuye 
wanga, kuti mundiyanje kwambiri". 

85. (Mulungu) adati: "Ndithu, 
Ife tawayesa Mayeso anthu ako 

1 Imam Zamakhashariyi adati: "Musa 
adazisankha zochokera mwa anthu ake, 
yomwe idaikidwa. Kenako iye adatsogoi 
chakhumbo ndi kufunitsitsa kumva mawu a 















pamodzi ndi nthumwi zomwe 
adamka kuphiri monga panyengo 
a nasiya m'buyo anthu chifukwa 
Mbuye wake". 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



671 



n *>« 



T • *J? 3jj-*i 



pambuyo pako; tero Samiriyu 
wawasokeretsa". ] 

86. Musa adabwerera kwa anthu 
ake ali Wokwiya ndi wodandaula. 
Adati :"E, inu anthu anga! Kodi 
Mbuye Wanu sadakulonjezeni 
lonjezo Labwino? Kapena nyengo 
yalonjezolo Idatalika kwa inu? 
Kapena mudafuna Kuti mkwiyo 
ukutsikireni Kuchokera kwa Mbuye 
wanu; Tero mwaswa lonjezo langa"? 

87. (I wo) adati: "Sitidaswe 
lonjezo lako Mwachifuniro chathu; 
koma Tidasenzetsedwa mitolo ya 
zodzikometsera Za anthu (ziwiya 
zagolide zomwe Tidabwereka kwa 
akazi a chimisiri), ndipo 
Tidaziponya (pamoto, ndipo 
Zidasungunuka ndikupangidwa 
mwana Wang'ombe. )Ndipo 
momwemonso Samiriyu Adaponya. 

88. Ndipo adawatulutsira 
(kuchokera M'golide 
wosungunukayo) mwana 
Wang'ombe wokhala ndi thupi 
lokwanira, Yemwe adali kulira: 
(iwo) adati: "Uyu ndi mulungu 
wanu ndiponso mulungu wa Musa, 
koma (Musa) Wamuiwala, (choncho 
wapita kukamfuna Kuphiri)!" 

89. Kodi sadaone kuti (mwana 
wang'ombe) Sabweza mawu kwa 



9&J2\J#%S%& 



't'Jij 'i Hi ^ *>**'< 












&$m^i&&%\ 



1 Samiriyu ameneyu adali wamatsenga, wachiphamaso (munafiku), wochokera 
kumtundu wa anthu opembedza ng'ombe. 



Siirat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



672 



n *>» 



Y • & 5jj*j 



iwo, ndiponso Sangathe kudzetsa 
matsautso kwa iwo Ngakhale 
zothandiza 

90. Ndipo Haaruna adawauza 
kale (kuti)" "E, inu anthu anga! 
Ndithu, inu Mwasokonezeka ndi 
(chinthu) ichi. Ndithu, Mbuye 
wanu ndi Mulungu Wachifundo 
chambiri; choncho Nditsateni, 
ndipo mverani lamulo langa, 
(Siyani kupembedza fano ili)." 

91. (Iwo) adati: "Sitisiya 
ngakhale Pang'ono kumpembedza. 
Kufikira Musa abwerere kwa ife," 

92. (Pamene Musa adabwerera) 
adati: "E, I we Haaruna! Nchiyani 
chidakuletsa Pamene udawaona 
atasokera, 

93. Kuti usanditsate? 
Udanyozera Lamulo langa?" 

94. (Haaruna) adati: E, iwe 
mwana Wa mayi anga! Usagwire 
ndevu Zanga,ngakhale mutu wanga 
(Poukoka chifukwa cha mkwiyo). 
Ndithu, ine ndidaopa (kuchoka ndi 
Ena, kusiya ena) kuti ungati: 
"Wawagawa ana a Israeli, ndipo 
Sudayembekezere mawu anga". 

95. (Musa) adati: "E, iwe 
Samiriyu! Nchiyani wachita?" 

96. (lye adati:) "Ndidaona 
zomwe Sadazione ndipo ndidatapa 
pang'ono Mapazi a Mtumiki 






k"> ,f\ '<' " 9 <> ' *\i>\£ 






jl \»9 9 "{\\' 9>9''\\C 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



673 n*>i 



t • At 



•-»-• 



ndikuwaponya (M'mwana wa 
ng'ombe). Ndipo Zimenezi ndi 
zomwe zidakomera Mtima wanga" 1 

97. (Musa) adati: " Choka, 
ndithu Pa iwe (pali chilango) 
pamoyo (wako) Choti uzingonena 
(kuti) Musandikhudze 
musandikhudze (Ndipo palibe 
amene Adzakuyandikira ndipo iwe 
Sudzayandikira aliyense). Ndithu, 
Pa iwe pali lonjezo la (Mulungu) 
Losaswedwa; ndipo muyang'ane 
mulungu Wako, yemwe wakhala 
Ukupitiriza kumpembedza. 
Timtentha, kenako chipala 
chakecho Tichiululutsa m'nyanja. 

98. Ndithu, wompembedza 
wanu, ndi Mulungu Yekha, 
Yemwe, palibe woti 
nkupembedzedwa Mwachoonadi 
koma lye. Ndipo wakwanira 
Pachilichonse kuchidziwa ndi 
nzeru (Zake zopanda malire). 

99. Umo ndi momwe 
tikukusimbira nkhani Za (zinthu) 
zomwe zidatsogola (za aneneri) 
Ndithu takupatsa uthenga waukulu 
kuchokera Kwa Ife (omwe ndi 
Qur'an). 






r^M^m^tk 






Samiriyu adaona Gabrieli ali kudza kwa Musa atakwera hatchi. Choncho 
adakondwera mumtima mwake kutapa mapazi ake. Tero ankati akaponya 
zomwe adatapazo pachinthu chilichonse chakufa chinkauka. Ndipo pamene 
fano la mwana wang'ombe lidakonzedwajye adatenga dothi la mapazi a 
mthengayo nkuponya pafanolo. Choncho fanolo lidayamba kulira ngati 
mwana wa ng'ombe. 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



674 



n *>» 



t • & o 



Ojf* 



100. Amene aunyozere, ndithu, 
iye tsiku La Kiyama adzasenza 
Mitolo (ya machimo); 

101. Adzakhala m'menemo 
(m'chilango) muyaya. Ndipo ndi 
zoipa zedi (kwa anthu) Kusenza 
mitolo (imeneyo) tsiku la Kiyama, 

102. (Kumbuka Mtumiki 
Muhammad {SAW}), tsiku Lomwe 
lipenga lidzaimbidwa. Ndipo 
Tidzasonkhanitsa oipa tsiku 
limenelo maso Awo ali a buluwu 
(chifukwa cha mantha). 

103. Adzanong'onezana pakati 
pawo (ponena Kuti): 
"Simudakhalitse padziko lapansi 
Koma masiku khumi okha basi". 

104. Ife tikudziwa kwambiri 
zimene azidzanena Pamene 
abwino awo pamayendedwe 
Azidzanena: "Inu simudakhale 
koma tsiku Limodzi basi 
(poyerekeza ndi kuchuluka Kwa 
masiku akumoto)". 

105. Ndipo akukufunsa 
zamapiri (kuti adzatani Tsiku la 
Kiyama); auze: "Mbuye wanga 
Adzawagumulagumula 
ndikuwaululutsa (Ngati fumbi) 

106. Ndipo adzaisiya (nthaka 
yonse) ngati Bwalo losalazidwa 
myaa!" 



'9' 9[ 9'i<»\'.9>' <' 9 19& 






&tSk403%&KZ 






mg$x&$te^ 






Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



675 



n *>» 



y * ^y *jj~* 



107. "Sudzaona kukhota 
m'menemo ngakhale Chitunda 
(chikweza)." 

108. Tsiku limenelo 
adzamtsatira woitana; Sadzatha 
kumpatuka, ndipo mawu 
(Azolengedwa) adzatonthola (Kuti 
chete) kwa (Mulungu) Wachifundo 
chambiri; Ndipo sudzamva, koma 
kunong'ona Basi, ndi migugu ya 
mapazi. 

109. Tsiku limenelo chiombolo 
(cha aliyense) Sichidzathandiza, 
kupatula yemwe Wapatsidwa 
chilolezo ndi (Mulungu) 
Wachifundo chambiri, ndi 
kumuyanja Kuti alankhule. 

110. (Mulungu) akudziwa 
Zapatsogolo pawo Ndizapambuyo 
pawo. Ndipo iwo Sangathe 
kumzindikira (Mulungu) Mmene 
alili. 

111. Ndipo nkhope (tsiku 
limenelo) Zidzalobodoka pamaso 
pa (Mulungu) Wamoyo 
Wamuyaya, Wochita Chilichonse. 
Ndithu, adzataika Kwathunthu 
yense wochita zosalungama. 

112. Ndipo amene achite 
zabwino uku ali Msilamu, 
sadzaopa kuchitiridwa zoipa 
Kapena kumchepetsera 
(Choyenera chake). 






&$&$&&&$& 
<&%&&&&% 






^G^aWSWS 



*Ql&& 






Siirat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



676 



n *>» 



t * & 



J>" 



113. Ndipo momwemo 
taivumbulutsa (Qur'an) 
m'Chiarabu ndipo tafotokoza 
M'menemo mwatsatanetsatane 
Zamachenjezo (amtundu 
uliwonse), Kuti aope (Mulungu), 
ndikuti Nthawi iliyonse 
(Qur'aniyo), iwapatse 
Chikumbutso Chatsopano. 

114. Watukuka Mulungu, 
Mfumu ya choonadi, Ndipo 
usaifulumizitse Qur'an 
(Powerenga) chivumbulutso chake 
Chisanamalizike kwa iwe, ndipo 
nena (Popempha) kuti: "Mbuye 
wanga! Ndionjezereni nzeru." 

115. Ndipo tidamulangiza 
(Mneneri) Adam Kale, koma 
adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa 
iye kulimba mtima (potsatira 
Lamulo lathu loti asadye zipatso za 
Mtengo woletsedwa). 

116. Ndipo (kumbukirani) 
pamene tidauza Angelo: 
"Muchitireni sajida (mulambireni 
Momulemekeza) Adam," ndipo 
adachita Sajida kupatula Iblis, 
Adakana. 

117. Tsono tidati: "E, iwe 
Adam! Ndithu, Uyu ndi mdani 
wako iwe ndi mkazi wako; 
Choncho asakutulutseni m'munda 
Wamtendere, mungadzavutike. 


















Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



677 n*>» 



Y * & ^jj- 1 ' 



118. Ndithu, iwe sumva njala 
M'menemo ndipo sukhala 
Wamaliseche, 

119. Ndipo iwe sumva ludzu 
m'menemo, Ndiponso sumva 
kutentha". 

120. Koma Satana 
(adamsokoneza) Pomunong'oneza 
(zoipa) adati: "E, Iwe Adam! Kodi 
ndikusonyeze Mtengo wamuyaya 
ndi (wopatsa) Ufumu wosatha?" 1 

121. Ndipo (onse awiri) 
adaudya, ndipo Umaliseche wawo 
awiriwo Udaonekera poyera; ndipo 
adayamba Kudziphatika masamba 
am'mundamo; Ndipo Adamu 
adalakwira Mbuye wake, choncho 
adasokera. 

122. Kenako Mbuye wake 
Adamsankha pomulandira kulapa 
Kwake ndikumuongola. 

123. (Mulungu) adati: 
"Chokani nonsenu M'menemo, 
uku pali chidani pakati Pa wina ndi 
mnzake, (padzakhala Chidani 
pakati pa ana anu); koma 
Chikadzakudzerani chiongoko 
Kuchokera kwa Ine, ndipo amene 
Adzachitsate chiongoko 



Satana wotembereredwa adanena kwa iye m'njira yachinyengo kuti: "Kodi 
iwe Adam, ndikusonyeze mtengo wakuti amene wadya zipatso zake, 
adzakhala muyaya wosafa ndikupeza ufumu wonkerankera mtsogolo, 
wosatha? Umo ndi momwe zidaliri ndate za satana. Sizidali zomufunira 
zabwino Adam, koma kumuononga. 






r? ] <^ \s*M&p3&^*^ 



©, 



^fwV4\ -'x\<'*\.<\ 



>J*i$. 



OJb 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



678 



>n *>» 



Y ♦ de Ojj** 



changacho, Sadzasokera ndiponso 
sadzavutika. 

124. Ndipo amene atanyozere 
ulaliki wanga, Ndithu, moyo 
wamavuto udzakhala pa lye ndipo 
tidzamuukitsa m'manda tsiku La 
chimaliziro ali wakhungu." 

125. Adzanena: "Mbuye 
wanga! Chifukwa ninji 
mwandiukitsa ndili Wakhungu, 
pomwe ndidali wopenya?" 

126. (Mulungu) adzanena: 
"Zimenezo Nchifukwa chakuti 
zidakudzera Aya zathu koma 
udaziiwala (Chifukwa 
chosalabadira), momwemo Lero 
uiwalidwa, (sulabadiridwa). 

127. Ndipo umo ndimomwe 
tidzamulipirire Aliyense wopyola 
malire, Wosakhulupirira aya za 
mbuye wake. Ndipo chilango cha 
tsiku la Chimaliziro nchaukali, 
ndiponso Chamuyaya. 

128. Kodi sizidadziwikebe kwa 
iwo kuti Ndi mibadwo ingati 
tidaiononga Patsogolo pawo? 
Ndipo awa (Osakhulupirira 
atsopano) akuyenda M'malo awo, 
(kodi saona zizindikiro 
Zakuonongeka kwawo)? Ndithu, 
NT zimenezo muli zisonyezo kwa 
eni Nzeru. 

129. Ndipo pakadapanda liwu 
lomwe Lidatsogola kuchokera kwa 












K^d&»&@$3#; 



Siirat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



679 



n *>i 



Y * aJp ^jj- - 



Mbuye wako (Lochedwetsera 
chilango) ndi nthawi Yomwe 
idaikidwa, ndithu (chilango) 
Chikadawafika (tsopano lomwe 
lino.) 

130. Pirira pazomwe 
akunenazo, ndipo Lemekeza 
Mbuye Wako ndi kumtamanda, 
Dzuwa lisanatuluke, ndiponso 
Lisanalowe; ndiponso nthawi 
zausiku Umulemekeze, ndi 
pakatikati pa usana; Kuti udzapeze 
zokukondweretsa (Tsiku la 
Kiyama). 

131. Ndipo usazitong'olere 
maso ako (Mozidololokera zinthu) 
zimene Tawasangalatsa nazo ena 
mwa anthu Pakati pawo; zimenezo 
nzokongoletsa Zamoyo wapadziko 
basi, kuti tiwayese Mayeso 
pazimenezo; koma chopatsa Cha 
Mbuye wako (chomwe 
Nchololedwa ngakhale chikhale 
Chochepa) nchabwino kwambiri 
Ndiponso chokhalitsa. 

132. Ndipo lamula banja lako 
kupemphera Swala ndi kuipirira 
iwe mwini swalayo 
Sitikukupempha riziki, (chakudya) 
Koma Ife ndi amene tikukudyetsa 
Ndipo malekezero abwino ali 
Mukuopa (Mulungu). 

133. Ndipo (osakhulupirira) 
adanena: "Chifukwa ninji 
sakutibweretsera Chizizwa 



rwj* 












&W&&$8&$\% 



Surat 20. Ta-Ha 



Juzu 16 



680 



n *>» 



V • & o 



ij^ 



kuchokera kwa Mbuye wake?" 
Kodi sudawafike umboni 
woonekera Wa zomwe zili 
m'mabuku akale? (Kodi 
sadakhutitsidwe ndi Qur'an 
Chomwe ndi chizizwa 
chachikulu)." 

134, Ndipo ngati 
tikadawaononga ndi Chilango, 
asanadze uyo (Mtumiki), 
Akadanena: "Mbuye wathu! 
Bwanji Osatitumizira mtumiki kuti 
titsate Aya zanu tisanayaluke ndi 
Kunyozeka?" 

135. Nena: "Aliyense (wa ife) 
Akuyembekezera (mphoto yake); 
Choncho yembekezerani. 
Posachedwapa mudziwa kuti kodi 
ndani Mwini njira yolingana, 
ndipo ndani amene Waongoka." 



«dS*«Ai^* 









l \'*\i 9 ) 9 '\ 9 * ^99<9^ '< 




Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 I 681 I W^i t \ tLJ^i Sj^-. 




SfjRAT AL-ANBIYA' XXI IjfiSs 

KgQ^^B^y^^.. — _ _ _; r ^^i..>-^^^^,-Jr..y.jj 



Surayi idavumbulutsidwa pambuyo pa Surati Ibrahim. Ndipo 
ikufotokoza za kuyandikira kwa Kiyama kumene Amshirikina 
ali kunyozera. Iwo akutinso mtumiki sangakhale munthu. Ndipo 
nthawi zina amati Qur'an ndi ufiti; nthawi zina nkumati ndi 
ndakatulo, nthawi zinanso amati ndi maloto osanganikira ndi 
kunama, pomwe chenjezo lili chiimire patsogolo pawo. Ndipo 
Aneneri adali anthu monga Muhammad (SAW). 

Anthu akale adakana Aneneri awo monga momwe Akuraishi 
adamkanira Muhammad(SAW). Koma Mulungu adaphwasula 
midzi yawo. Ndithu, lye ngokhoza kuononga, ndiponso 
ngokhoza kuisiya kuti inkerenkere mtsogolo. Ndipo chilichonse 
chakumwamba ndi pansi ncha lye. Ndipo angelo m'makwerero 
awo, amalemekeza Mulungu; safooka. 

Ndithu, kulingana ndi kukhala bwino kwa thambo ndi nthaka, 
ndichisonyezo chakuti amene adazipanga zimenezi ndi 
m'modzi. Ndipo akadamthandiza aliyense, zikadaonongeka. 

Ndipo aneneri onse adadza ndi ulaliki wopembedza Mulungu 
m'modzi. lye alibe mwana. Ndipo aliyense wa iwo sanena kuti 
iye ndi mnzake wa Mulungu. Ngati atatero ndiye kuti mphoto 
yake ndi Jahena. 

Mulungu Woyera wafotokoza zakukula kwa zolengedwa 
Zake ndikudodometsa kwa kalengedwe ka thambo ndi nthaka. 
Ndipo wafotokozanso chikhalidwe cha Amshirikina ndi 
osakhulupirira. Kenaka wapitiriza kunenanso kuti Iye ndi amene 
amasunga anthu. Ndipo walongosolanso za mphoto ya 
osakhulupirira pa tsiku la chiweruzilo (Kiyama) ndipo 
wakambanso nkhani ya Musa ndi Haaruna pamodzi ndi Farawo, 
komanso ya Ibrahim pamodzi ndi anthu ake.Zakuti adamdalitsa 
ndi ana abwino. Tsono Chauta wakambanso za Luti ndi anthu 
ake ndi kuonongeka kwawo. Ndipo wakambanso za Nuhu ndi 
kusakhulupirira kwa anthu ake; ndi kuwaononga onse psiti, 



Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



682 



VV «.j*-i 



T ^ *L-/!M 3jj-» 



kupatula amene adakhulupirira. Wapitiriza Mulungu kukambanso 
za Sulaiman, Daudi, Ayub, Ismaila, Idrisi, Zili Kifl, Zi Nnun ndi 
Maryam. 

Ndipo surayi yafotokozanso za nkhani ya Yaajuju ndi 
Maajuju. kenako Mulungu wafotokoza za ntchito yabwino ndi 
zipatso zake ndi zomwe adzawalipire omwe aopa ndikuchita 
zabwino, ndi momwe adzakhalire pa tsiku la chimaliziro 
(Kiyama). Ndipo wafotokozanso kuti Uthenga wa Muhammad 
(SAW) ndi Mtendere kwa zolengedwa, ndikuti zinthu zonse 
nzake Mulungu. Ndipo lye Ngoweruza bwino kuposa oweruza 
ena onse. 




Siirat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 I 683 1 1 v *>i 



Y> *Ui^5j>- 



SuratAl-Anbiya'XXI 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Chiwerengero chayandikira 
kwa anthu Pomwe iwo ali 
m'kusalabadirandi M'kunyozera. 

2. Palibe pamene ukuwadzera 
ulaliki Watsopano wochokera kwa 
Mbuye wawo Koma 
amaumvetsera uku akuchita 
Zachibwana, 

3. Mitima yawo ikunyozera 
(osalabadira Zakudza kwa 
Kiyama). Ndipo Akunenezana 
mobisa amene adzichitira Zoipa; 
(akuuzana motere:) "Kodi uyu 
(Muhammadiyu) ndi ndani, 
simunthu Monga inu? Kodi 
mukuudzera ufiti Pomwe 
mukuuona?" 

4. (Mneneri 
Muhammad {SAW}) adati: 
"Mbuye wanga akudziwa zimene 
Zikunenedwa kumwamba ndi 
pansi; Ndipo lye Ngwakumva; 
Ngodziwa. 

5. Koma (osakhulupirira) adati: 
"(Izi Zimene akufotokozazi) ndi 
maloto Opanda pake." (Ndipo 
nthawi zina Amati:)"Koma 
zimenezi wazipeka." (Penanso 
amati:) "Koma iyeyu Ndi 



#, 






o£*3\^3^J9- 



£> 









i*M$&\<X&&$$ 



Q *'V4P& 






Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 684 * V ^ 



t \ ;USl Oj>- 



Mlakatuli. Chonchotu, 
atibweretsere Chizizwa monga 
mmene adatumiziridwa (Aneneri) 
oyamba." 

6. Sadakhulupirire apatsogolo 
pawo, eni Midzi imene 
tidaiononga (ngakhale Kuti 
zozizwitsa adaziona); nanga Iwo 
akhulupirira? 

7. Ndipo sitidawatume 
patsogolo pako, ( Iwe Mtumiki,) 
koma anthu, (Osati Angelo); 
tidawavumbulutsira 
(Chivumbulutso Chathu.) 
Choncho, Afunseni eni kudziwa 
ngati Inu simukudziwa (nkhani 
zakale). 

8. Ndipo sitidawachite 
(Aneneriwo) kukhala Matupi 
osadya chakudya ndipo Sadalinso 
amuyaya. 

9. Kenako tidawatsimikizira 
lonjezo (Lakuwathangata pa adani 
awo), ndipo Tidawapulumutsa iwo 
ndi amene Tidawafuna (mwa 
omwe adawatsata), Ndipo olumpha 
malire (a Mulungu) 
Tidawaononga. 

10. Ndithu, tatumiza kwa inu 
Buku lomwe M'kati mwake muli 
ulaliki wanu (Malangizo kwa inu). 
Kodi simukuzindikira? 

11. Ndi ambiri mwa eni midzi 
yomwe idali Yosalungama, 






X&\£$CJ6^} 



9\?"\" 



%&$$#% 






wt%w$®$$\& 



%$&&Z'0^\Z^& 



Siirat 21. AI-Anbiya' Juzu 17 685 ^ V t>i 



T > frLJ^I «j>-> 



tidawaononga; ndipo Pambuyo 
pake tidalenga anthu ena. 

12. Pamene adazindikira Za 
chilango chathu, Pompo adayamba 
kuchithawa. 

13. Musathawe, ( kuthawa 
Sikukupulumutsani), koma 
bwererani Kuzimene 
mwasangalatsidwa Nazo ndi 
m'malo mwanu, kuti Mufunsidwe. 

14. Adanena: "Tsoka lathu 
ndithu, tidali Ochita zoipa". 

15. Kukuwa kwawoko 
sikudathe, kufikira Tidawapanga 
ngati (mbewu) Zokololedwa, 
mpaka kupuma kwawo Kudazima 
(adafa). 

16. Ndipo sitidalenge thambo 
ndi nthaka Ndi zapakati pake, 
mwamasewera. 

17. Tikadafuna kupanga choti 
tiziseweretsa (Sitidakapanga 
zomwe mukuzionazi) Koma 
tikadapanga mwazomwe tili nazo, 
Tikadakhala ochita zachibwana. 

18. Koma (chimene timachita 
ndi ichi), Timachiponya choona pa 
chachabe ndi Kuchiswa bongo 
bwake, ndipo Chachabecho 
chimachoka. Ndipo Chilango chili 
pa inu chifukwa cha Zomwe 
mukunena (Kumnamizira 
Mulungu). 






©U- 



'M>>~J<rw.<.\ 






®< 



'9 ^ \* !> ' 









Surat 21. AI-Anbiya' Juzu 17 686 > V *>i 



t ^ frW^ 1 5 jj-» 



19. Onse akumwamba ndi 
pansi, Ngake (Mulungu); ndipo 
amene ali kwa lye (Angelo), 
sadzitukumula Pakumulambira, 
ndiponso satopa (Ndi 
mapemphero) 

20. Amamlemekeza usiku ndi 
usana,ndipo Sagwidwa ndi ulesi. 

21. Kapena adzipangira 
milungu yochokera M'nthaka 
youkitsa akufa, (kotero kuti 
Aichita kukhala milungu yawo 
mmalo Mwa Mulungu)? 

22. Kukadakhala kuti ilipo 
M'menemo milungu ina 
(kuthambo ndi Pansi) kupatula 
Mulungu, (ziwirizi) 
Zikadawonongeka, wapatukana 
Mulungu Mbuye wa mpando 
Wachifumu ndi zimene akunena 
(Osakhulupirira). 

23. Safunsidwa pazimene 
akuchita, Koma iwo adzafunsidwa. 

24. Kapena adzipangira 
milungu ina M'malo mwa lye? 
Nena: "Bweretsani Umboni wanu 
(pazimenezi), (Izi ndikuuzani) 
ndichikumbutso kwa Awa ali 
pamodzi ndi ine, ndiponso 
Ndichikumbutso kwa amene 
adalipo Patsogolo panga." Koma 
ambiri a iwo Sadziwa zachoonadi, 
tero iwo Akunyozera. 












Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 I 687 h V *>i 



X ^ *A~^M «jj-» 



25. Ndipo sitidatume patsogolo 
pako Mneneri aliyense koma tidali 
Kumzindikiritsa kuti palibe 
Mulungu Wina wompembedza 
mwachoonadi, Koma Ine; choncho 
ndilambireni. 

26. Ndipo (osakhulupirira) 
akuti: "(Mulungu) Wachifundo 
chambiri wadzipangira Mwana." 
Mulungu wapatukana (ndi 
Zimenezo) koma (awa angelo) ndi 
akapolo (A Mulungu) amene 
alemekezedwa. 

27. Samtsogolera kulankhula, 
ndipo iwo Amachita molingana ndi 
malamulo Ake. 

28. (Mulungu) akudziwa 
zapatsogolo pawo (Angelowo) ndi 
zapambuyo pawo,ndipo 
(Angelowo) sangaombole 
(aliyense) Koma yekhayo 
(Mulungu) wamuyanja, Ndipo 
iwo, chifukwa chomuopa, 
Amanjenjemera. 

29. Ndipo mwa iwo amene 
anganene kuti: "Ine ndi mulungu 
mmalo mwa lye," Ndiye kuti 
timulipira Jahannama; umo Ndi 
momwe timawalipirira ochita 
zoipa. 

30. Kodi osakhulupirira 
sadaone kuti Thambo ndi nthaka 
Zidali zophatikizana, Ndipo 
tidazilekanitsa? Ndipo ndi madzi 












111 1 -*.*. 9 > 9 » ( 9\W#\ »* 9 \K& 9 " 






Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



688 



W *>i 



t 1 *LJ^ 5jJ~» 



Tidalenga chilichonse chamoyo. 
Kodi Sakhulupirira? 

31. Ndipo tidaika mapiri 
panthaka Molimbika kuti 
isagwedezeke ndi iwo, Ndipo 
m'menemo tidaikamo misewu 
Kuti alondole njira (Ndikufika 
komwe afuna). 

32. Ndipo thambo tidalipanga 
monga Tsindwi losungidwa (kuti 
lisagwe): Koma iwo 
akuzitembenukira kumbali 
Zizindikiro zake. 

33. Ndipo lye ndi Yemwe 
adalenga usiku ndi Usana, dzuwa 
ndi mwezi; chilichonse Mwa izo 
chikusambira mozungulira M 'njira 
mwake. 

34. Ife sitidawachite anthu 
amene adalipo Patsogolo pako 
kukhala amuyaya. Nanga Ukafa, 
kodi iwo adzakhala muyaya? 

35. Chamoyo chilichonse 
chidzalawa imfa; Ndipo 
tikukuyesani mayeso ndi zinthu 
Zoipa ndi zabwino. Ndipo nonsenu 
Mudzabwezedwa kwalfe. 

36. Ndipo amene 
sadakhulupirire akakuona, 
Akungokuchitira chipongwe. 
"Kodi Ndi uyu yemwe akutchula 
milungu yanu (Mwachipongwe)?" 
Pomwe iwo ndi Amene akukana 















***) 












Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 689 I ^ V *>i 



Y > frLJ^I 5jj-- 



zakutchula (Mulungu) Wachifundo 
Chambiri. 

37. Munthu walengedwa ndi 
chikhalidwe Chokonda zinthu 
(zake zonse) Mwachangu. 
Posachedwapa Ndikusonyezani 
zisonyezo Zanga; choncho 
musandifulumizitse 
(Kukubweretserani chilango 
changa) 

38. Ndipo (osakhulupirira) 
akuti: "Kodi Malonjezo awa 
adzakwaniritsidwa liti, Ngati 
mukunena zoona?". 

39. Chikhala kuti amene 
sadakhulupirire Akudziwa 
chilango chimene Chidzawapeza 
panthawi yomwe Sangathe 
kutchinjiriza moto kunkhope Zawo 
ndi kumisana yawo ndipo kuti 
Sadzathandizidwa, (sakadanena 
Zimenezi.) 

40. Koma (Kiyama) 
idzawadzera Mwadzidzidzi ndi 
kuwadzidzimutsa; Ndipo kenako 
sadzatha kuibweza Kapena 
kupatsidwa danga (kuti achite 
Zomwe sadachite.) 

41. Ndipo ndithu, Atumiki 
adachitidwa Chipongwe patsogolo 
pako; choncho Amene adachita 
chipongwe mwa iwo, Zidawadzera 
zomwe adali kuzichita Chipongwe. 









1 -•"' 



©U&x* 






f 9J*J'*'"Z t. '*' 9 9 *\* 9\' 






9S 



(3^<i^^L^^^^^ 



u 



ysi>\c»>\ \»f."> 



A *' 9 9 9*9* 



Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 I 690 I S V *>t 



T > frW^ 1 *jj~» 



42. Nena: "Kodi ndani 
angakutetezeni usiku Ndi usana ku 
masautso a (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri?" Koma 
iwo Akunyozera kukumbuka 
Mbuye wawo. 

43. Kapena ali nayo milungu 
yowatchinjiriza M'malo mwa Ife? 
(Milunguyo) siingathe 
Kudzithandiza yokha (nanga ndiye 
Ingathe kuthandiza ena?) Ndipo 
(Milungu) imeneyo 
siidzasamalidwa Ndi Ife. 

44. Koma awa (osakhulupirira) 
Tidawasangalatsa ndi Makolo awo 
kufikira Nthawi ya moyo wawo 
idatalika; kodi Saona kuti 
tikulidzera dziko lawo 
Ndikulichepetsa malire ake?. 
Nanga kodi iwo ndiwo opambana? 

45. Nena: "Ndithu, 
ndikukuchenjezani ndi 
Chivumbulutso (cha Mulungu). 
"Koma Agonthi samva kuitana 
pamene Akuchenjezedwa". 

46. Ndipo kukadawakhudza 
kumenya kumodzi Kwa chilango 
cha Mbuye wako, Ndithudi, 
(akadadzichepetsa nthawi 
Yomweyo). Akadanena: "Tsoka 
kwa Ife ndithu,tidali osalungama". 

47. Ndipo tsiku la Kiyama 
tidzaika masikero Achilungamo, 
choncho mzimu uliwonse 



9 <*' V. 9' *S 9i' h \'<>\\ 






\S99 ** ?* K 9'9$g'*i 9,<*< 









-^\^\&&\>& 



Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 I 691 ) V ^jJfc-i 



t > *lj^ 5^ 



Sudzachitidwa chinyengo pa 
Chilichonse.Ngakhale 
(chinthucho) Chili cholemera ngati 
njere ya mpiru, Tidzachibweretsa; 
ndipo tikukwana (Kukhala 
akatswiri) pa chiwerengero. 

48. Ndipo ndithu, Musa ndi 
Haaruna Tidawapatsa (buku) 
losiyanitsa pakati Pachoonadi ndi 
chonama, ndiponso muuni Ndi 
ulaliki kwa anthu Oopa Mulungu 

49. Omwe akumuopa Mbuye 
wawo Ngakhale ali paokha, 
omwenso Amaopa Kiyama. 

50. Ndipo iyi (Qur'an) ndi 
ulaliki Wodalitsidwa umene 
tauvumbulutsa (kwa Inu); kodi inu 
mukuikana? 

51. Ndipo ndithu, Ibrahim 
tidampatsa Kulungama kuyambira 
kale (kuubwana), Ndipo 
tinkamudziwa (bwinobwino). 

52. (Akumbutse anthu) pamene 
adauza A bambo ake ndi anthu 
ake, "Nchiyani mafano awa omwe 
inu Nthawi zonse mukupitiriza 
Kuwapembedza." 

53. Adati: "Tidapeza makolo 
athu Akuwapembedza.(Choncho 
nafenso Tikuwapembedza)". 

54. (lye) adati: "Ndithu, inu ndi 
makolo Anu mudali mkusokera 
koonekera." 









*** "x^ V-**^ £&**'** <i#^ 



9 l'\}"9 \»fo9S\3'<" 









Surat 21. AI-Anbiya' Juzu 17 692 ^ V *>i 



r ^ tu^i oj^-. 



55. (Iwo) adati: "Kodi 
watibweretsera Choonadi, kapena 
iwe ndi m'modzi Mwa osereula?" 

56. (lye) adati: ("Iyayi, ine 
siwosereula), Koma Mbuye wanu, 
ndi Mbuye Wathambo ndi nthaka 
amene adalenga Zimenezi; ine 
pazimenezi, ndine M'modzi 
wochitira umboni". 

57. "Ndipo ndikulumbirira 
Chauta, Ndiwachitira chiwembu 
mafano Anuwo pambuyo 
ponditembenukira Misana kupita 
komwe mukupita." 

58. Choncho adawaphwanya 
(mafanowo), Zidutswazidutswa 
kupatula lalikulu lawo (Sadaliswe) 
kuti iwo alibwerere (ndi Kulifunsa 
zimene zachitika). 

59. (Iwo pamene adafika 
kumafano awo) Adati: "Ndani 
wachita ichi pa Milungu yathu? 
Ndithu, iye ndi M'modzi waochita 
zoipa." 

60. Adati: "Tidamumva 
m'nyamata wina Akuitchula 
(moipa); amatchedwa Ibrahim." 

61. Adati: "Mubweretseni 
pamaso Pa anthu kuti amuone." 

62. Adati: "Kodi ndiwedi 
Wachita ichi ku milungu yathu, 
Ee, iwe Ibrahim?" 



\' 9 






<36%$Z\lZ\ooS&$6j 



®(j&j£$j$ 






Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



693 



W*>l 



t > *Ljty 5j>-» 



63. (lye) adati: "(Iyayi), koma 
wachita Ichi ndi mkulu wawoyu. 
Choncho Afunseni (kuti akuuzeni 
zenizeni) Ngati amatha 
kuyankhula." 

64. Ndipo adadzitembenukira 
okha Ndikunena kuti: "Ndithu, inu 
ndinu Oipa." 

65. Kenako adazyolitsa mitu 
yawo (Ndikubwerera kuumbuli 
wawo) Nanena kuti, "Ndithu, iwe 
ukudziwa Kuti izi siziyankhula 
(nchifukwa ninji Ukutichita 
chipongwe)?" 

66. (lye) adati: "Kodi 
mukupembedza Zomwe 
sizingakuthandizeni chilichonse, 
Kusiya Mulungu, zomwenso 
Sizingakupatseni masautso?" 

67. "Kuyaluka nkwanu ndi 
zomwe Mukuzipembedzazo kusiya 
Mulungu. Kodi simuganizira?" 

68. (Iwo) adati: "Mtentheni; 
ndipo pulumutsani Milungu yanu, 
ngati inu mungathe Kuchita 
zimenezi." 

69. Tidati: "E, iwe Moto! Khala 
kuzizira Ndiponso mtendere kwa 
Ibrahim". 

70. Ndipo adamfunira 
chiwembu; koma Tidawachita 
kukhala otaika zedi. 









© 



Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



694 



W *>i 



t > f-W^' *j>-» 



71. Ndipo tidampulumutsa iye 
ndi Luti kupita kudziko lomwe 
tidalidalitsa Ku zolengedwa. 

72. Ndipo (Ibrahim) tidampatsa 
Isihaka ndi Kuonjezera Yakubu, 
ndipo tidawachita Onse kukhala 
abwino. 

73. Ndipo tidawasankha 
Kukhala atsogoleri, Owongolera 
mwalamulo lathu, ndipo 
Tidawazindikiritsa kuchita 
zabwino ndi Kupemphera swala, 
ndi kupereka Zakat; ndipo adali 
odzichepetsa kwa Ife. 

74. Ndipo Luti tidampatsa 
luntha ndi Kuzindikira, ndipo 
tidampulumutsa Kumudzi womwe 
Anthu ake ankachita Zoipa; ndithu 
iwo adali anthu oipa Otuluka 
m'chilamulo (cha Mulungu). 

75. Ndipo tidamulowetsa 
kuchifundo chathu; Ndithu, iye 
adali m'modzi waochita Zabwino. 

76. Ndipo (akumbutse za) Nuhi, 
pamene Adatiitana kale 
(kutipempha). Ndipo Ife 
tidamuyankha ndi kupulumutsa iye 
Ndi anthu ake kusautso lalikulu. 

77. Ndipo tidampulumutsa pa 
anthu amene Adatsutsa aya zathu; 
ndithu, iwo adali Anthu oipa. 
Ndipo onse tidawamiza (Ndi 
chigumula chamadzi). 






© 



(^QZ$S'j%& 












Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



695 



W fr>» 



t ^ s-W*^ ^JJ— 



78. Ndipo (akumbutse za) 
Daudi ndi Sulaiman, Pamene 
ankaweruza mlandu wa munda 
Pomwe mbuzi za anthu zidadya 
ndi Kuonongaononga usiku 
mmenemo ndipo Ife tidali mboni 
pa kuweruza kwawo. 

79. Tidamzindikiritsa za 
mlanduwo Sulaiman (kuposa tate 
wake Daudi). Yense waiwo 
tidampatsa kuweruza Mwaluntha 
ndi kudziwa; ndipo Tidagonjetsa 
mapiri ndi mbalame kuti Zikhale 
pamodzi ndi Daudi Zikulemekeza 
Mulungu; ndithu, Ife ndi ochita 
chimene tafuna. 

80. Ndipo tidamphunzitsa 
(Daudi) kapangidwe Kachovala 
chapankhondo chifukwa Cha inu 
kuti chikutetezeni mkumenyana 
Kwanu; kodi simungakhale 
othokoza? 

81. Nayenso Sulaiman 
tidamufewetsera mphepo 
Yamphamvu; inkayenda 
mwalamulo lake Kunka kudziko 
lomwe talidalitsa (Dziko la 
Shamu); ndipo Ife pa Chilichonse 
Ngodziwa. 

82. Ndipo (tidamufewetseranso) 
Asatana Omwe ankamubirira 
m'madzi (Ndikumtolera ngale), 
ndipo ankachita Ntchito zina 
kuonjezera pa zimenezi; Ndipo Ife 
tidali owalondera. 















Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 696 > V *>) 



t > *W»SM 3j>*- 



83. Ndipo akumbutsenso za 
Ayubu pamene Adakuwira Mbuye 
wake (kuti); "Ndithu mavuto 
andikhudza, pomwe Inu Ndi 
Achifundo kuposa achifundo!" 

84. Choncho tidavomera 
(pempho lake); ndipo 
Tidamchotsera mavuto omwe adali 
Nawo, ndipo tidampatsa ana ake 
Ofanana ndi omwe adali nawo kale 
Ndikuonjezeranso ena onga iwo, 
(Zonsezi monga) chifundo 
chochokera Kwa Ife, (ndikuti 
zikhale) chikumbutso Kwa ochita 
mapemphero. 

85. Ndipo (mutchule) Isimaila 
ndi Idrisa Ndi Zul Kifli, onsewa 
adali Mwa opirira; 

86. Tidawalowetsanso 
kuchifundo chathu, Ndithu, iwo 
adali mwa Anthu abwino. 

87. Ndipo (mutchulenso) Zun- 
nun (Yunusu), Pamene adachoka 
uku atakwiya, ndipo Ankaganiza 
(kuti tamuloleza kusamuka) 
Ndikuti sititha kumchita kanthu. 
Choncho Adaitana mumdima 
(wam'mimba Mwansomba imene 
idamumeza, kuti): "Ndithu, palibe 
mulungu wina Wopembezedwa 
mwachoonadi koma Inu; 
mwayeretsedwa; ndithu, ine 
ndidali M'modzi wa odzichitira 
zoipa." 






© 






©<i^oJ!^ 



Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 597 > V *>i 



Y ^ *LJ^ ojj^ 



88. Choncho tidavomereza 
(pempho lake) ndi Kumpulumutsa 
ku madandaulo; umo ndi M'mene 
timapulumutsira okhulupirira. 

89. Ndipo (akumbutse za) 
Zakariya pamene Adaitana Mbuye 
wake (kuti): "Mbuye Wanga! 
Musandisiye ndekha; Ndithu, Inu 
ndinu wabwino kuposa alowa 
mmalo Onse." 

90. Choncho tidamuvomera 
(pempho), Ndikumpatsa Yahaya 
ndikumkonzera Mkazi wake. 
Ndithu iwo adali achangu Pochita 
zabwino; ankatipempha 
Mwakhumbo ndi mwamantha, 
Ndipo adali Odzichepetsa kwa Ife. 

91. Ndipo (atchulire za mkazi) 
yemwe Adauteteza umaliseche 
wake (pozisunga); Ndipo tidauzira 
mwa iye Mzimu Wathu, Ndipo 
tidamchita iye ndi mwana Wake 
kukhala chizizwa (cha Mulungu) 
Kwa zolengedwa zonse. 

92. Ndithu, uwu mpingo wanu, 
ndimpingo Umodzi, ndipo Ine 
ndine Mbuye wanu; Choncho 
ndipembedzeni. 

93. Koma iwo adaswa chinthu 
chawochi Pakati pawo (tero 
adakhala mipingo 
Yosiyanasiyana). Onse 
adzabwerera kwa Ife. 



9*< "Xti ^ 9< 9* ? < ' 






© (ift-^^ 1 






%3p 



Surat 21. AI-Anbiya' Juzu 17 



698 



W*jJt-i 



T 1 frLJ^l ojj~- 



94. Ndipo amene achite ntchito 
zabwino Uku ali Msilamu, khama 
lake Silidzakanidwa; ndithunso, Ife 
Tikumlembera zonse zimene 
akuchita. 

95. Ndipo nkosatheka kwa eni 
mudzi umene Tidauononga 
chifukwa cha machimo Awo kuti 
asabwerere kwa Ife; (Koma ndithu 
abwerera). 

96. Kufikira pamene (mpanda 
wa) Yaajuju Ndi Maajuju 
adzatsekulidwa, ndipo Iwo 
adzakhala akuthamanga kuchokera 
M'phiri lililonse. 

97. Ndipo lonjezo lachoonadi 
Lidzafika; pamenepo maso a 
omwe Sadakhulupirire, 
adzatong'oka Uku akunena: 
"Tsoka pa ife. Ndithu, tidali 
osalabadira (zachinthu) Ichi; koma 
tidali oipa, (odzichitira tokha 
Zoipa.") 

98. Ndithu, inu ndi amene 
Mukuwapembedza kusiya 
Mulungu, Ndinu nkhuni za ku 
Jahannama. Ndipo inu 
(Jahannamayo) mudzaifika. 

99. Ngati awa akadakhala 
milungu Yeniyeni, ndiye kuti 
sakadaifika (Sakadailowa) 
mmenemo onse adzakhala 
muyaya. 









<zs'A >.& " Vs 9* 









Surat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



699 



W*j*-» 



t > ^ljVi Ojf 



100. Mmenemo iwo adzakhala 
akubuula Ndipo iwo mmenemo 
sadzamva (Chifukwa makutu 
adzagontha). 

101. Ndithu, amene ubwino 
wathu Udawafika, iwo 
adzatalikitsidwa nawo (Motowo). 

102. Sadzamva mavume ake, 
ndipo iwo Adzakhala muyaya 
m'zomwe Ikukhumba mitima 
yawo. 

103. Kugwedezeka kwakukulu 
Sikudzawadandaulitsa; Ndipo 
angelo adzawalandira 
(Ndikuwauza): "Hi ndi tsiku lanu 
Lomwe mudali kulonjezedwa." 

104. Tsiku lomwe tidzakulunga 
thambo Monga momwe 
amakulungira makalata Okhala ndi 
malembo m'kati mwake; Monga 
tidayamba kulenga Zolengedwa 
poyamba, Tidzabwerezanso 
(kuzilenga kachiwiri. Ndipo 
aliyense adzalipidwa pazomwe 
Adali kuchita) ili ndilonjezo 
lomwe Lili pa Ife. Ndithu, Ife ndi 
Ochita (zomwe tikunena.) 

105. Ndipo ndithu, tidalemba 
m'zaburi (M'masalimo buku la 
Daudi) pambuyo Polemba mu 
Lauhil-Mahafudh Kuti:"Dziko 
(lapansi) adzalilowa Akapolo 
Anga abwino." 






^ 'iXp^ ^h^' (!£&*$ 









Siirat 21. Al-Anbiya' Juzu 17 



700 



W frjJfe-i 



Y 1 *W^H 5 j>- 



106. Ndithu, pazimenezi 
(nkhani za aneneri), Pali miyambo 
kwa anthu, opembedza (Mulungu). 

107. Ndipo sitidakutume koma 
kuti ukhale Mtendere kwa 
zolengedwa zonse. 

108. Nena: "Ndithu, 
kukuvumbulutsidwa Kwa ine kuti 
Mulungu wanu ndi Mulungu 
mmodzi; nanga inu Mudzagonjera 
(zofuna Zake Polowa 
m'Chisilamu)?" 

109. Koma ngati anyozera, 
nena: "Ndalengeza Uthenga kwa 
inu Mofanana (popanda tsankho); 
Sindidziwa kuti zomwe 
Mukulonjezedwa zili pafupi 
Kapena zili kutali. 

110. "Ndithu, lye akudziwa 
mawu Okweza, ndiponso 
akudziwa zomwe Mukubisa. 

111. "Ndipo sindikudziwa, 
mwina Kuchedwetsa chilango 
chanu ndi mayeso Akukuyesani 
ndikukusangalatsani Ndi zokoma 
(za M'dziko) mpaka Idzakwane 
nthawi yoikidwayo." 

112. Adati: "E, Mbuye wanga. 
Weruzani moona." "Ndipo Mbuye 
Wathu ndi (Mulungu) Wachifundo 
Chambiri; wopemphedwa 
chithandizo Pazimene 
mukusimbazo." 



®<i#^^>$ ^mI^Uu! 



*&£j3fc2hM3fcj 















Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 701 W *jJH 



tt 



r^t a^j-*** 



SURAT AL-HAJJ XXII 



t==^ 




Surayi yayamba ndi nkhani yoopseza kwambiri, yomwe 
inganjenjemeretse mitima ndi kuchotsa nzeru chifukwa 
chakuopsa kwake. Ndipo kumeneko ndiko kugwedezeka kwa 
dziko mwamphamvu komwe kudzachitika patsogolo patsiku la 
Kiyama. 

Kugwedezeka sikudzakhala kwa mapiri ndi nyumba basi, 
koma kudzakhalanso amayi oyamwitsa ndi amayi apakati kotero 
kuti oyamwitsa sadzalabadira za ana awo; naonso apakati 
adzataya pakati pawo nthawi isadakwane. Ndipo anthu 
adzakhala ali dzandidzandi ngati aledzera ndi mowa. Sikuti 
aledzera ndi mowa, koma kugwedezeka koopsa kwadziko 
komwe nkonjenjemeretsa mitima kwambiri. 

Surayi ikufotokozanso za zizindikiro zosonyeza kuuka ku 
imfa ndi kunka kunyumba yolandirira mphoto kuti munthu 
akalandire mphoto yake; mphoto ya chabwino, njabwino, 
mphoto ya choipa, njoipa. 

Surayi ikulongosolanso za maonekedwe a tsiku la Kiyama: 
abwino adzakhala ku nyumba ya mtendere ndipo oipa adzakhala 
kunyumba yachilango cha moto. 




Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



702 



\V *jk-\ 



YY 



g^ l5 J>* 



Surat Al-Hajj XXII 



y 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. E, inu anthu! Opani Mbuye 
wanu (ndipo Kumbukirani tsiku la 
Kiyama). Ndithu, Kugwedezeka 
kwa Kiyama ndichinthu 
Chachikulu (kwabasi). 

2. Tsiku limene mudzaione 
(Kiyamayo), Mkazi aliyense 
woyamwitsa adzaiwala (Mwana 
wake) womuyamwitsa, ndipo 
(Mkazi) aliyense wapakati 
adzataya Pakati pake; ndipo 
udzawaona anthu Ataledzera, 
pomwe sadaledzere; koma Ndi 
chilango chaukali cha Mulungu 
(Chimene chawapeza). 

3. Ndipo alipo ena mwa Anthu 
amene akutsutsa Za Mulungu 
popanda Kuzindikira, ndipo 
akutsatira Satana aliyense 
wolakwa. 

4. (Za Satana), kwalembedwa 
kuti amene Amsankhe kukhala 
bwenzi lake, ndithujye 
amsokeretsa ndi kumtsogolera 
Kuchilango cha moto. 

5. E, inu anthu ngati muli 
m'chikaiko zakuuka ku Imfa, 
(ndipo mukuona kuti nzosatheka, 
Yang'anani mmene 



feVi 



■ - 



Q^I^I^W- 



-£> 


















Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 703 > V *>» 



XY 



g^ 5 ^ 



tidakulengerani). Ndithujfe 
tidakulengani ndi dothi, ndipo 
(Timakulengani) ndi dontho la 
umuna, komanso (Umunawo 
udasanduka) gawo lamagazi, 
Kenako gawo la mnofii 
woumbidwa (chithunzi 
Chamunthu) ndi wosaumbidwa, 
kuti Tikulongosolereni (kukhoza 
kwathu;) ndipo Ife 
Timachikhazikitsa mchiberekero; 
chimene Tifuna kufikira nthawi 
yake yoyikidwa kenako 
Timakutulutsani muli khanda, 
(tsono Timakulerani) kuti mufike 
pamsinkhu wanu. Ndipo ena mwa 
inu amamwalira (asanakule) 
Pomwe ena mwa inu 
amabwezedwa kumoyo Wofooka 
(waukalamba) kotero kuti 
asadziwe Chilichonse pambuyo 
pakuti adali wodziwa. Ndipo 
umaiona nthaka ili chetee, koma 
Tikatsitsa madzi pamwamba pake, 
imagwedezeka Ndi kufufuma, ndi 
kumeretsa mtundu Uliwonse wa 
mmera wokongola. 1 

6. Zimenezo (monga kulenga 
munthu ndi kumeretsa Mmera, ndi 
umboni wosonyeza) kuti Mulungu 
Woona alipo; ndikuti iye 









1 Munthu amene ali ndi chikaiko zakuuka kuimfa, pafunika kuti aganizire 
zomwe zili m'ndime iyi yolemekezeka kuti aone komwe wachokera ndi komwe 
wafika. Kenako aone nthaka polingalira mozama momwe imakhalira yachilala. 
Koma mvula ikaivumbwira ndikudzuka, kuti adziwe kuti amene akuchita 
zimenezi palibe chomwe angalephere. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



704 



1V*j*-l 



tt 



S^ 5 J>* 



amaukitsa akufa, Ndiponso lye ali 
ndi mphamvu pachilichonse. 

7. Ndipo, ndithu, Kiyama 
idza;palibe Chikaiko pazimenezi, 
ndipo ndithu, Mulungu 
adzawatulutsa amene ali m'manda. 

8. Ndipo alipo mwa anthu 
amene akutsutsa za Mulungu 
popanda kuzindikira, Ngakhale 
chiongoko, ndi Buku lounika, 
(Koma makani basi ndi kungotsata 
zimene Akuziganizira). 1 

9. (Yemwe) akupinda khosi 
lake (chifukwa Chodzikuza) kuti 
asokeze (anthu powachotsa) 
Kunjira ya Mulungu; pa iye pali 
chilango Choyalutsa pamoyo uno, 
ndipo patsiku la Kiyama 
tikamulawitsa chilango chamoto 
Wotentha. 

10. (Tidzamuuza kuti): "Izi ndi 
zomwe Manja ako adatsogoza; 
ndithu, Mulungu siwachinyengo 
kwa akapolo (Ake)." 

11. Ndipo alipo wina mwa 
anthu amene Akupembedza 
Mulungu cham'mphepete 
(Mwachipembedzo). Chabwino 












1 Kutsutsana pa zinthu za chipembedzo popanda kudziwa ndi kukhala ndi 
umboni wokwanira.nkoletsedwa zedi. 

Maphunziro enieni amene angamzindikiritse munthu za chipembedzo, ndi 
omwe akupezeka m'Qur'an ndi m'mahadisi a Mtumiki (Mtendere ndi madalitso 
a Mulungu akhale pa iye) omwe ali oona, ndi maphunziro amene akupezeka 
m'mabuku ophunzitsa malamulo achipembedzo omwe ali ovomerezeka ndi 
atsogoleri a Chisilamu, osati buku lililonse lolembedwa ndi munthu wamba. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



705 



W*>» 



tt 



e^*j>* 



chikampeza Amatonthola nacho; 
koma masautso akamufika, 
Amatembenuka ndi nkhope yake 
(posiya Chikhulupiriro mwa 
Mulungu. Choncho) Waluza moyo 
wadziko lapansi ndi moyo wa tsiku 
La chimaliziro; kumeneko ndiko 
kuluza Koonekera. 1 

12. M'malo mwa Mulungu, 
amapembedza zomwe 
Sizingampatse masautso (ngati 
ataleka Kuzipembedza), ndiponso 
zomwe Sizingampatse chithandizo 
(akamazipembedza) Ndipo 
kumeneko ndiko kusokera 
kwakukulu. 

13. Akupembedza omwe 
masautso awo ali Pafupi zedi 
poyerekeza ndi zabwino zawo, 
Taonani kuipa atetezi ndiponso ndi 
abwenzi oipa. 

14. Ndithu, Mulungu 
adzalowetsa kuminda Yamtendere 
amene akhulupirira Ndikuchita 
zabwino, mitsinje ikuyenda Pansi 
(pa mindayo). Ndithu, Mulungu 
Amachita chimene wafuna. 

15. Amene akuganiza kuti 
Mulungu Samthangata (Mtumiki 
wake) padziko Lapansi ndi patsiku 



<%$<®3&<ty*£fo 









Mulungu watibweretsa pano padziko lapansi kuti tiyesedwe mayeso 
akulungama ndi kusalungama tsiku tomaliza lisanadze. Choncho tipirire ndi 
kugwiritsa zimene Mulungu ndi Mtumiki Wake atiuza. Tidziwe kuti pali mavuto 
pali zabwino. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 706 ^ V ^jA-i 



rr 



g^ 5 j>" 



la chimaliziro, Amange chingwe 
kudenga, kenako Adzipachike 
(ngati safuna kuona Chisilamu 
chikufala); ndipo aone Kuti kodi 
ndale zakezo zichotsa Zimene 
zamkwiitsazo? 

16. Momwemonso taitumiza 
(Qur'an) kuti Ikhale mawu 
omveka; ndipo ndithu, Mulungu 
amaongola amene wamfiina. 

17. Ndithu, amene akhulupirira, 
ndi Amene ali m'chipembedzo cha 
Chiyuda, Ndi chipembedzo cha 
Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi 
(opembedza moto), Ndi 
ophatikiza Mulungu ndi mafano, 
Ndithu, Mulungu adzaweruza 
pakati pawo Tsiku la chiweruziro 
(Kiyama). (Osokera 
Adzaponyedwa kumoto ndipo 
olungama Adzalowetsedwa 
kumunda wamtendere). Ndithu, 
Mulungu ndi mboni pachinthu 
Chilichonse. 

18. Kodi suona kuti Mulungu 
Zikumulambira zimene zili 
Kumwamba ndi zimene zili 
M'nthaka, kudzanso dzuwa, 
Mwezi,nyenyezi mapiri, mitengo, 
Nyama ndi anthu ambiri. Koma 
ambirinso chilango chatsimikizika 
Pa iwo. Ndipo amene Mulungu 
wamuyalutsa, Palibe amene 
angampatse ulemerero; ndithu, 
Mulungu amachita chimene wafiina. 






u®fcs$$&$&$& 












Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



707 



>V^>» 



rr 



s^ 5 j>- 



19. Awa ndi magulu awiri 
amene akangana pa za Mbuye 
wawo (pa zomwe zili zomuyenera, 
ndi Zosamuyenera, ndipo ena 
sadakhulupirire.) Choncho amene 
sadakhulupirire, adzawadulira 
Nsalu za kumoto ndi kuwaveka; 
ndipo Pamwamba pa mitu yawo 
padzathiridwa madzi Otentha. 

20. Chifukwa chamadziwo 
zidzasungunuka Zomwe zili 
m'mimba mwawo Ndiponso 
makungu (awo). 

21. Ndipo (kuonjezera 
pazimenezi) adzakhala nazo 
Nyundo zachitsulo (zowamenyera.) 

22. Nthawi iliyonse akafuna 
kutuluka M'menemo, chifukwa 
chakumva kupweteka, 
Adzabwezedwa momwemo (ndipo 
angelo uku Akuwamenya ndi 
nyundo), ndi (kuwauza): 
"Chilaweni chilango chootcha". 

23. Ndithu, Mulungu 
adzalowetsa amene Akhulupirira 
ndi kumachita zabwino, Kuminda 
ya mtendere komwe mitsinje 
ikuyenda Pansi pake; m'menemo 
akavekedwa (ndi Angelo) zibangili 
za golide ndi ngale; Ndipo zovala 
zawo m'menemo Zidzakhala za 
veleveti. 

24. Ndipo adzatsogozedwa 
(kupita kumalo) Kokamba mawu 






^»S*Wvi« 









Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



708 



W tjA-i 



1 1 gJ-1 5jj^» 



abwino okhaokha; ndiponso 
Adzatsogozedwa kunjira ya Mwini 
Kutamandidwa (kunjira yonkera 
ku Janna). 

25. Ndithu, amene 
sadakhulupirire (Mulungu Ndi 
Mtumiki Wake) ndipo 
nkumatsekereza Ena kunjira ya 
Mulungu, (ndiponso 
Nkumatsekereza kulowa) mu 
Msikiti Wopatulika umene 
tidauchita kuti ukhale Wa anthu 
onse mofanana kwa amene 
akukhala M'menemo ndi kwa 
alendo, (anthu otere tidzawalanga 
ndi chilango chaukali), Ndipo 
aliyense wofiina kuchita zopotoka 
M'menemo mosalungama, 
timulawitsa Chilango chowawa 
zedi. 

26. Ndipo (kumbukira) pamene 
tidamkhazika Ibrahim (ndi 
kumlondolera) pamalo Pa Nyumba 
(Yopatulikayo; tidamuuza Kuti): 
"Usandiphatikize ndi chilichonse; 
Ndipo iyeretse nyumba yanga 
chifukwa Cha amene 
akuizungulira ndi kumakhala 
Pompo (pochita mapemphero 
awo); ndi Omwe amawerama ndi 
kugwetsa nkhope Zawo pansi. 1 



e^lil^JtSiSdE 









Mulungu akuuza Mtumiki Muhammad (SAW) kuti akambire opembedza 
mafano zankhani ya Ibrahim yemwe iwo amati akumutsata pakupembedza 
kwawo mafano ndi kuichita nyumba yopatulikayo kukhala nyumba 
yopembedzera mafano kuti Ibrahim tidamulondolera pamalo anyumbayo ndi 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 [ 709 | \ V *£\ 



TY 



^hy* 



27. Ndipo (tidamuuza): 
"Lengeza kwa Anthu za Haji; 
akudzera (ena) oyenda Ndi 
mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba 
pa Chiweto choonda (chiflikwa 
chamasautso A paulendo); adza 
kuchokera kunjira Zamtalimtali; 

28. Kuti adzaone zabwino 
zawo, ndikuti (Achulukitse) 
kutchula dzina la Mulungu 
m'masiku odziwika (ubwino 
Wake), kupyolera m'zimene 
wawapatsa Monga ziweto za 
miyendo inayi. Ndipo Idyani ina 
mwa nyamayo ndi kum'dyetsa 
Wovutika, wosauka. 

29. Kenako adziyeretse 
kuzitakataka zawo, Ndipo 
akwaniritse naziri (malonjezo) 
Zawo ndikuzungulira nyumba 
yakale." 

30. Umo ndi momwe zikhalire; 
ndipo amene Alemekeze zinthu 
zopatulika za Mulungu Kutero ndi 
bwino kwa iyeyo pamaso pa 
Mbuye Wake. Ndipo ziweto za 
miyendo inayi Nzovomerezeka 
kwa inu kuzidya, kupatula Zomwe 
zatchulidwa kwa inu (m'Qur'an 
kuti Nzoletsedwa); choncho 






<*>, 



W5» 









kumlamula kuti aimange ndikuti asandiphatikize pamapemphero ndi china 
chilichonse, ndikuti aiyeretse nyumba Yanga kuuve wamafano ndi uve wina 
uliwonse kuti pakhale pamaio pozungulira chifukwa choopa Mulungu. Nanga 
bwanji iwo apasankha kukhala popembedzera mafano. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



710 



W *>i 



YY 



S^'JJ- 



Upeweni uve wa mafano,Ndiponso 
pewani mawu abodza, 

31. Uku mutapendekera kwa 
Mulungu Yekha, osati 
kum'phatikiza (Mulungu). Ndipo 
amene Akuphatikiza Mulungu Ndi 
mafano, ali ngati wogwa 
Kuchokera kumwamba, kenako 
Mbalame nkumuwakha, kapena 
Mphepo kukamtaya malo akutali. 

32. Zimenezo ndikuti amene 
alemekeze Zizindikiro za 
chipembedzo cha Mulungu, kutero 
ndichinthu choonetsa Kuopa 
Mulungu m'mitima. 

33. (Ziweto zimene 
mukutumiza ku Makka monga 
Nsembe) muli nazo zithandizo 
mmenemo (Monga kuzikwera ndi 
kuzikama mkaka) Kufikira nthawi 
yodziwika, (yomwe ndi nthawi 
Yozizingira); kenako malo 
ozizingira ndi pafupi Ndi nyumba 
yakalekaleyo. 

34. Ndipo mpingo uliwonse 
tidaupangira malo Ozingira 
nsembe zamapemphero kuti 
Atchule dzina la Mulungu pa 
zomwe Wawapatsa monga ziweto 
zamiyendo Inayi. Choncho 
Mulungu wanu ndi Mulungu 
m'modzi Yekha; gonjerani kwa 
lye; Ndipo odzichepetsa auze 






©i 



9 * *S,S 






6* *>'*> \"i^\\>S'S\'\ 9 i 









Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



711 



w *>i 



YT 



«JM Sjj— » 



nkhaniyabwino. 1 

35. Omwe Mulungu 
akatchulidwa, Mitima yawo 
imanjenjemera ndiponso 
Amapirira pazomwe zawapeza, 
ndipo Amapemphera swala 
moyenera Ndi kupereka chopereka 
kuchokera m'zomwe Tawapatsa. 

36. Ndipo ngamira (ng'ombe, 
mbuzi ndi Mberere) tadzichita kwa 
inu kuti zikhale Mwazizindikiro za 
chipembedzo cha Mulungu; 
m'zimenezo Muli zabwino kwa 
inu; choncho Litchuleni Dzina la 
Mulungu pa izo Pamene zikuima 
mondanda (uku Mukuzizinga,) 
ndipo zikagwa Cham'nthiti, idyani 
(nyama yake) Ndikumdyetsa 
yemwe Akungozungulirazungulira, 
Wosapempha ndi wopempha 
yemwe. Momwemo tazigonjetsa 
kwa inu (Pochita kuti 
zikugonjereni) Kuti muthokoze. 

37. (Nyamazo) Mulungu 
siimfika minofu yake Ngakhale 
magazi ake, koma kuopa 
kuchokera Mwa inu ndiko kumene 
kumamfika; momwemo 
Wazikhalitsa (nyamazo) zogonjera 
inu kuti Mumlemekeze Mulungu 












1 Tanthauzo la ndime iyi nkuti malamulo a za Haji sadaikidwe pa inu nokha 
Asilamu, koma mpingo uliwonse wokhulupirira Mulungu adauikira malo ndi 
malamulo operekera nsembe zawo kwa Mulungu kuti atamande dzina Lake 
ndi kum'lemekeza pozinga nsembezo, monga kumthokoza lye pazimene 
wawapatsa. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



712 



W*>l 



YY 



S^ l5 J>" 



chifukwa Chakukuongolaniku. 
Auze nkhani yabwino Ochita 
zabwino. 

38. Ndithu, Mulungu 
amawateteza amene Akhulupirira, 
ndithu, Mulungu sakonda Aliyense 
wachinyengo, wosathokoza. 

39. Chaperekedwa chilolezo 
kwa (Asilamu) Amene akuputidwa 
(ndi Adani awo kuti abwezere) 
chifukwa chakuti iwo Achitiridwa 
zoipa; ndipo ndithu, Mulungu 
Ngokhoza kuwathandiza; 

40. Omwe atulutsidwa 
m'nyumba zawo popanda 
Chilungamo, koma pachifiikwa 
chakuti Akunena, "Mbuye wathu 
ndi Mulungu. "Ndipo Pakapanda 
Mulungu kukankha anthu ena 
Kupyolera mwa ena, (popatsa ena 
mphamvu Kuti agonjetse ena), 
ndiye kuti Masinagogi, 
Matchalitchi, nyumba Zina 
zopemphereramo Ndi misikiti 
momwe dzina la Mulungu 
Likutchulidwa mochuluka 
zikadagumulidwa. Ndithu, 
Mulungu am'thangata amene 
Akuthangata chipembedzo Chake; 
ndithu, Mulungu Ngwanyonga, 
Wogonjetsa chilichonse. 









M'ndime iyi, Mulungu akuti akadawalekerera anthu oipa, omwe cholinga 
chawo nkudzetsa chisokonezo padziko, popanda kusankha anthu ena kuti 
alimbane nawo, ndiye kuti nyumba zopemphereramo Ayuda, Akhrisitu ndi 
Asilamu, zikadagumulidwa. Koma Mulungu amasankha anthu olungama kuti 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



713 



W *>i 



Y Y g^l 5jj-» 



41. Omwe akuti tikawakhazika 
padziko Mwa ubwino, amachita 
Mapemphero a swala Moyenera 
ndi kupereka zakat, Ndi kulamula 
zabwino ndi kuletsa zoipa; Ndipo 
mabwerero a zinthu Nkwa 
Mulungu basi. 

42. Ndipo ngati akukuyesa 
wabodza, (awa Akafiri, 
sizachilendo), ndithu, 
Adatsutsanso (aneneri awo) 
patsogolo Pawo anthu a Nuhi, 
Aadi, a Samudu, 

43. Anthu a Ibrahima, anthu a 
Luti, 

44. Ndi anthu a ku Madiyani; 
Nayenso Musa adayesedwa 
Wabodza (adamkana). Ndipo 
Osakhulupirira Ndidawapatsa 
nthawi, Kenako ndidawathira 
dzanja. Nanga Chidali bwanji 
chilango changa. 

45. Ndi midzi ingati 
tidaiononga yomwe inkachita 
Zoipa? Zipupa zitagwera pa 
madenga ake. Ndipo ndi zitsime 
(zingati) zomwe Zidasiidwa, ndi 
nyumba zikuluzikulu Zomwe 
zidali zolimba? 

46. Kodi sayendayenda padziko 

kuti akhale Ndi mitima (yanzeru) 






9?} 9£ 99'9£ 9 " <i'/ 9 *< "\9*"'?>9iS 



^as^aa 



£' 









&$%u&JM%£® 



alimbane ndi anthu oipawo kuti choonadi cha Mulungu chisazime. Ndipo 
amene akuteteza choonadi cha Mulungu, Chauta walonjeza kumthangata. 



Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



714 



W*>i 



YY 



g^ 1 8 J>* 



yowazindikiritsa Ndi makutu 
omvera? Ndithu, maso Sagwidwa 
khungu, (khungu loononga 
Chipembedzo), koma mitima 
yomwe ili M'zifiiwa ndi imene 
imagwidwa khungu (Loononga 
chipembedzo). 

47. Ndipo akukufulumizitsa 
kuti udzetse Chilango. Komatu 
Mulungu sadzaswa Lonjezo lake 
(limene adaliika lakuti Chilango 
chenicheni chidzakhala patsiku La 
chimaliziro). Ndipo ndithu, tsiku 
Limodzi kwa Mbuye wako lili 
ngati zaka Chikwi chimodzi 
mukawerengedwe kanu. 

48. Kodi ndi (anthu) amidzi 
ingati amene Ndidawapatsa nthawi 
pomwe ankachita Zoipa? Kenako 
ndidawathira m'dzanja.Ndipo kwa 
lye nkobwerera. 

49. Nena: "E, inu anthu! 
Ndithu, ine Kwa inu ndine 
Mchenjezi woonekera:" 

50. "Tsono amene akhulupirira 
ndi kumachita Zabwino, 
chikhululuko ndi riziki Laulemu 
zili pa iwo." 

51. "Ndipo amene akulimbika 
Kulimbana ndi aya zathu, Iwo wo 
ndi anthu a kumoto." 

52. Ndipo palibe pamene 
Tidatuma Mtumiki ngakhale 
M'neneri patsogolo pako, koma 















(J&9W9 &0& wSI^ 






Surat 22. Al-Haj j Juzu 1 7 



715 



W ^j*-i 



n 



g^ s j>" 



Akamawerenga, satana amaponya 
(Zosokoneza) m'kuwerenga 
kwakeko; Koma Mulungu 
amachotsa zomwe satana 
Akuponya; kenako nkuzilongosola 
aya Zake. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa Kwambiri, Wanzeru 
zakuya. 

53. (Izi zimachitika) kuti 
achichite Chimene satana 
akuponya kukhala Mayeso kwa 
omwe m'mitima mwawo muli 
Matenda ndi ouma mitima yawo; 
ndithu, Osalungama ali 
m'kusiyana komwe kuli Kutali 
(ndi choonadi); 

54. Ndipo kuti adziwe amene 
apatsidwa Kuzindikira kuti 
chimeneehi N'choonadi 
chochokera kwa Mbuye Wako ndi 
kuchikhulupirira ndikuti Mitima 
yawo idzichepetse kwa lye; 
Ndithu, Mulungu ndi Woongolera 
ku Njira yolunjika amene 
akhulupirira. 

55. Ndipo amene 
sadakhulupirire apitirira Kukhala 
m'chikaiko ndi chimenecho 
(Wadza nachocho) kufikira tsiku la 
Chimaliziro liwadzera 
mowatutumutsa, Kapena 
chiwadzera chilango pa tsiku 
Lopanda chabwino (kwa iwo). 

56. Ufumu tsiku limenelo ngwa 
Mulungu; adzaweruza 



n, '% 









@ *# 






^%fe 






h9 2£ZK"\ 






Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



716 



W $->! 



t Y gJ-l 5jj-» 



(mwachilungamo) Pakati pawo; 
choncho amene Akhulupirira ndi 
kumachita Zabwino, adzakhala 
m'minda yamtendere. 

57. Ndipo amene 
sadakhulupirire (Mulungu Ndi 
Mtumiki Wake) ndikutsutsa aya 
Zathu, iwo adzapeza chilango 
choyalutsa. 

58. Ndipo amene asamuka 
chifukwa cha Chipembedzo cha 
Mulungu, kenako Ndikuphedwa 
kapena kufa, ndithu, Mulungu 
adzawapatsa (patsiku la 
Chiweruzo) zopatsa zabwino. 
Ndithu, Mulungu Ngwabwino 
popatsa Kuposa opatsa. 

59. Ndithu, adzawalowetsa 
pamalo pom we Adzapayanja. 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa; 
Ngodekha 

60. Zimenezi zili chonchi, 
ndipo yemwe Akubwezera kulanga 
molingana ndi momwe lye 
adalangidwira; kenakonso 
nkuchitidwa Mtopola, ndithu, 
Mulungu amthangata; Mulungu 
Ngofufuta uchimo; Wokhululuka 
Kwambiri. 

61. Zimenezo nchifukwa 
chakuti Mulungu Amalowetsa 
usiku mu usana ndikulowetsa 
Usana mu usiku, ndi chifukwanso 












® &?*•■« 









i^ia^^^tel^ 



'4>\&s$\a'J$\& 



is£ 






Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



717 



W*>» 



tt 



g^ i5 J>^ 



Chakuti ndithu Mulungu 
Ngwakumva Ngopenya. 

62. Zimenezo nchifukwa 
chakuti Mulungu ndi Wowona 
(Alipo;) ndipo zimene 
akuzipembedza Kusiya lye, 
nzachabe. Ndipo Mulungu 
Ngwapamwambamwamba 
Ngwamkulu. 

63. Kodi suona kuti Mulungu 
amatsitsa Madzi kuchokera 
kumitambo, ndipo Nthaka 
imakhala yobiriwira? Ndithu, 
Mulungu Ngodziwa zobisika 
ndiponso Ngodziwa zoonekera. 

64. Zakumwamba ndi zapansi 
zonse Nzake; Ndithu, Mulungu 
Ngwachikwanekwane; 
Wotamandidwa. 

65. Kodi sudaone kuti Mulungu 
Wakufewetserani zonse 
zam'nthaka Ndi zombo zomwe 
zikuyenda panyanja Mwalamulo 
Lake? Ndipo wagwira thambo Kuti 
lisagwe panthaka koma kupyolera 
M'chilolezo Chake; ndithu, 
Mulungu Ngodekha kwa anthu 
Ngwachifundo. 

66. Ndipo lye ndi Amene 
adakupatsani Moyo; kenako 
adzakupatsani imfa, Ndipo kenako 
adzakuukitsani; Ndithu, munthu 
ngosathokoza . 












© 



$> 



si&> 






Surat 22. AI-Hajj Juzu 17 718 1 V *>» 



Y T gJ-l 5j^ 



67. Mpingo uliwonse tidauikira 
Machitidwe amapemphero omwe 
Akuwatsata; choncho asatsutsane 
Nawe pachinthu ichi, ndipo itanira 
Anthu ku chipembedzo cha Mbuye 
Wako. Ndithu, iwe uli 
pachiongoko Chenicheni . 

68. Ndipo ngati atsutsana nawe, 
nena: "Mulungu Wodziwa koposa 
zimene Mukuchita." 

69. "Mulungu adzaweruza 
pakati panu Tsiku la Kiyama 
pazimene mudali Kusiyana." 

70. Kodi sudziwa kuti Mulungu 
akudziwa Zakumwamba ndi 
zapansi? Ndithu, Zonsezo zili 
m'kaundula (Wake), Ndithu, 
(kudziwika kwa) zimenezo kwa 
Mulungu nzosavuta. 

71. Ndipo akupembedza 
milungu yabodza, Kusiya 
Mulungu, yomwe (Mulungu) 
Sadaitumizire umboni wakuti 
(Ipembedzedwe) yomwenso iwo 
Sakuidziwa bwino. Ndipo anthu 
Osalungama sadzakhala Ndi 
owathandiza. 

72. Koma aya zathu zomveka 
Zikawerengedwa kwa iwo, uona 
Kunyansidwa pankhope za Amene 
sadakhulupirire. Ndipo amakhala 
Pafupi kuwamenya amene 
Amawawerengera aya zathu. 
Nena: "Kodi ndikuuzeni zoipa 












*Vi<9*i\' At 99 9 ' * $99" 

©4*4 &&ito 









Siirat 22. Al-Hajj Juzu 17 



719 



W *>i 



YY 



g^ 1 5 J>^ 



kwambiri Kuposa izi? Ndi moto 
(Wa Mulungu) umene 
wawalonjeza amene 
Sadakhulupirire (Mulungu ndi 
Mtumiki Wake) amenewo ndi 
mabwerero oipa zedi." 

73. E, inu anthu! Fanizo 
laperekedwa; Choncho limvereni. 
Ndithu, amene Mukuwapembedza 
m'malo mwa Mulungu, Sangathe 
kulenga ntchentche ngakhale 
Atasonkhana (kuti athandizane) 
Pachimenechi. Ndipo ngati 
ntchenche Itawalanda chinthu, 
sangathe kuchilanda 
Kuntchentcheyo. Wafooka 
kwenikweni Wopempha ndi 
wopemphedwa. 

74. Sadamlemekeze Mulungu, 
kulemekeza Komuyenera. Ndithu, 
Mulungu Ngwamphamvu 
Ngogonjetsa chilichonse. 

75. Mulungu amasankha 
atumiki mwa angelo Ndi mwa 
anthu. Ndithu, Mulungu 
Ngwakumva; Ngopenya. 

76. Akudziwa zimene zili 
patsogolo pawo Ndi zimene zili 
pambuyo pawo; kwa Mulungu 
Yekha ndiko kobwerera Zinthu. 

77. E, inu amene 
mwakhulupirira! Weramani 
ndikugwetsa nkhope zanu pansi 
Ndipo mpembedzeni Mbuye wanu 



o%K^S&^^t*olS 



£- ?9 "1 






9 * i} '* 






Surat 22. Al-Hajj Juzu 17 



720 



W tjtr\ 



t T gj-l 5jj^» 



Ndikuchita zabwino kuti 
mupambane. 

78. Ndipo menyerani 
chipembedzo cha Mulungu, 
kumenyera kwa choonadi; lye ndi 
Amene adakusankhani (kuti 
Mukhale mpingo wabwino;) ndipo 
Sadaike pa inu zinthu zolemera 
Pachipembedzo, ndi chipembedzo 
Cha tate wanu Ibrahim. lye 
(Mulungu) Adakutchani Asilamu 
kuyambira kale (M'mabuku akale) 
ndi mu iyi, (Qur'an) kuti Mtumiki 
akhale mboni Pa inu, inunso kuti 
mukhale mboni Pa anthu. Choncho 
pempherani swala; Perekani zakat 
ndipo gwirizanani Chifukwa cha 
Mulungu. lye ndiye Mbuye wanu, 
Mbuye wabwino zedi, Ndi 
Mthandizi wabwino zedi. 







Surat 23. Al-Mu'miniin Juzu 18 



721 



^A *>» 



YT Oji*jll ^J-" 




Surayi yayamba ndi kunenetsa zakupambana kwa 
okhulupirira. Ndipo yatsatiza ndi kufotokoza mbiri zawo. 
Kenako yafotokotoza chiyambi chakulengedwa kwa munthu ndi 
maonekedwe osonyeza kukhoza kwa Mulungu 
Wapamwambamwamba. Ndipo yatsatiza pankhaniyi nkhani za 
aneneri zomwe zikuonetsa kuti uthenga wawo udali wofanana 
ndikutinso anthu ngochokera kukholo limodzi. 

Surayi yafotokoza za yemwe akufuna chiongoko ndi mwini 
kusokera. Ndipo yasimbanso za maganizo a "Amshirikina" pa 
za M'neneri Muhammad (Mtendere ndi Madalitso a Mulungu 
zikhale pa iye). Ndipo Mulungu m'surayi wafunsamo mafunso 
kuti anthu amuyankhe molingana ndi chilengedwe chawo. 

Kenako surayi yasimba za momwe anthu adzakhalira pa tsiku 
la Kiyama (Chimaliziro) ponenetsa kuti iwo adzaweruzidwa 
mwachilungamo. 




Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 722 ^A t^ IT dyspoj^ 



Sural Al-Mu 'minim XXIII 






M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Ndithu apambana 
okhulupirira (Mwa Mulungu ndi 
Atumiki Ake) 

2. Amene amakhudzumuka 
Pamapemphero awo (poipereka 
mitima Yawo kwa Mulungu 
modzichepetsa). 

3. Ndi omwe amapewa zinthu 
Zopanda pake (zachabe). 

4. Ndi omwe amakwaniritsa 
(Nsanamira ya) chopereka (Zakat). 

5. Ndi omwe amasunga 
umaliseche wawo. 

6. Kupatula kwa akazi Awo ndi 
adzakazi omwe Manja awo 
akumanja apeza. Choncho iwo 
(pakukumana ndi amenewo) Saali 
odzudzulidwa 

7. Koma omwe angafune 
zosemphana ndi izi (Kulumikizana 
ndi mkazi posiya njira Ziwirizi) 
iwowo ndiwo opyola malire (A 
Mulungu). 

8. Ndi amene amasunga 
malonjezo awo ndi Zomwe 
akhulupirika nazo; 



Ojfe&\<&&\&\j 



^ 



&&#\?&\& 



^^U^^SA 






'? A'**'*®' 






t&$a^&&& 



Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



723 



\ A frji-l Y V O^pjil djj-*. 



9. Ndi omwe akusunga 
Mapemphero awo (popemphera 
m'nthawi Zake ndi kutsata malamulo 
ake uku Ali odzichepetsa). 

10. Iwo ndi olandira (zabwino 
tsiku la Kiyama). 

11. Amene adzalandira Munda 
wa Mtendere (Wotchedwa) 
Fir'dausi (Munda Wapamwamba 
kwambiri). M'menemo iwo 
Adzakhala muyaya. 

12. Ndipo ndithu, Tidamlenga 
munthu Kuchokera ku dongo 
labwino; 

13. Kenako tidalenga ana ake 
ndi dontho Lamadzi (Ambewu ya 
munthu) lomwe Lidaikidwa 
pamalo osungidwa; 

14. Kenako tidalisintha 
dontholo kukhala Magazi oundana; 
ndipo kenako magaziwo 
Tidawasintha kukhala m'nofu; 
ndipo Kenako m'nofu tidausintha 
kukhala Mafupa; ndipo mafupawo 
tidawaveka Minofu, kenako 
tidamsintha kukhala Cholengedwa 
china. Choncho, watukuka 
Mulungu, Wabwino polenga. 

15. Kenako ndithu inu pambuyo 
Pazimenezo mudzamwalira 

16. Ndithu inu, kenako 
mudzaukitsidwa Pa tsiku la 
Kiyama. 






(a\".'->,\\ 









© 



"»-iiTi >''■ 









Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



724 h A *>i 



Tf Oj^jil &jj-» 



17. Ndipo ndithu, tapanga njira 
(mitambo) Zisanu ndi ziwiri 
pamwamba panu, Ndipo 
ndithu,(Ife) sitisiya kulabadira 
Zolengedwa. 

18. Ndipo tatsitsa madzi 
mwamuyeso Kuchokera 
kumwamba, ndi Kuwakhazikitsa 
m'nthaka; ndipo ndithu Ife ndi 
okhoza kuwachotsa (kuti 
Musathandizike nawo koma 
Sitidachite zimenezo chifukwa 
Chokuchitirani chifundo). 

19. Ndi madzi amenewo, 
tidakupangirani Minda ya kanjedza 
ndi mpesa, M'menemo inu 
mulinazo zipatso Zambiri; ndipo 
Mwazimenezo mumadya. 

20. Ndipo (adakupangirani) 
mtengo Womera paphiri la Sinai, 
womwe Umatulutsa mafuta; ndipo 
ndindiwo Kwa amene amadya. 
(Mtengo wake ndi mzitona). 

21. Ndipo ndithu, m'ziweto 
Muli lingaliro kwa inu. 
Timakumwetsani zomwe zili 
m'mimba Mwake; ndipo 
m'zimenezo mukupeza Zothandiza 
zambiri; ndipo zina mwaizo 
Mumadya. 

22. Ndipo pa msana pa izo ndi 
Pamwamba pazombo, 
mumanyamulidwa. 



<&tiffifolS@@x&> 









©^ 






©; 



*&MM9!& 



Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



725 hA *j*-i 



YT J^»jil *jj*** 



23. Ndipo ndithu, tidamtuma 
Nuhi kwa anthu Ake, ndipo adati: 
"E, inu anthu anga! Mpembedzeni 
Mulungu! Mulibe mulungu Wina 
woti nkumpembedza kupatula lye. 
Kodi simuopa (chilango Chake?) 

24. Akuluakulu mwa anthu ake 
amene Sadakhulupirire, adati: 
"Uyu sali kanthu, Koma ndi 
munthu ngati inu; akufuna kuti 
Adzipezere ubwino pa inu; ndipo 
Mulungu akadafuna 
(kukuphunzitsani) Akadatuma 
angelo. Zoterezi sitidamvepo 
Kumakolo athu akale". 

25. "Uyu sali kanthu, koma ndi 
munthu Wamisala; choncho 
muyembekezereni Mpaka nthawi 
(yofera".) 

26. (Nuhi) adati: "Mbuye 
wanga; Ndipulumutseni pakuti 
anditsutsa!" 

27. Choncho 
tidamuvumbulutsira (Mawu 
Akuti): "Panga chombo 
moyang'aniridwa 
Ndikudziwitsidwa ndi Ife". Ndipo 
Lamulo Lathu likadza 
ndikufwamphuka Madzi muuvuni, 
lowetsa mkati mwake 
(Mwachombocho) chilichonse 
Ziwiriziwiri, chachimuna ndi 
chachikazi Ndi banja lako, 
kupatula yemwe liwu Latsogola pa 









'>JXs&*-*fi\>'<Si'L' 



9 It*" 






Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



726 h A *>i 



TT Oji^jll $jj-> 



iye kuti aonongeke mwa iwo. 
Ndipo usandilankhule Za omwe 
adzichitira (okha) zoipa Ndithu 
iwo amizidwa (m'madzi). 

28. Ndipo ukakhazikika 
m'chombocho, iwe Ndi amene uli 
nawo, nenani: "Tikuthokoza 
Mulungu, amene Watipulumutsa 
ku anthu Osalungama". 

29. Ndipo (potsika),nena: "E, 
Mbuye wanga! Nditsitseni; 
kutsitsa kwa madalitso, Pakuti Inu 
ndinu wotsitsa bwino kwambiri 
Kuposa otsitsa". 

30. Ndithu, m'zimenezi muli 
zisonyezo. Ndithu, Ife tili (ndi 
udindo) wowayesa ndi mayeso 
Osiyanasiyana. 

31. Kenako tidabweretsa 
m'badwo wina pambuyo Pawo 
(omwe ndi Adi). 

32. Ndipo tidatuma kwa iwo 
m'neneri (Hudu) Wochokera mwa 
iwo, (yemwe ankati): "Pembedzani 
Mulungu! Mulibe mulungu wina 
Kupatula Iye. Kodi simuopa? 

33. Ndipo akuluakulu a mwa 
anthu ake amene Adali 
osakhulupirira, ndikutsutsa za 
Kukumana ndi tsiku la chimaliziro, 
omwe Tidawapatsa kulemera 
pamoyo wapadziko, Adati: "Uyu 
saali kanthu, koma ndi Munthu 






j. 



r "' iz &iup, ». \ .?r „ < »a. " 



Jk^ij 



%^m*8<M>'oM 









& 



Surat 23. AI-Mu'minun Juzu 18 



727 



\ A ftjA-1 f V ji* jil 5jj--» 



monga inu; amadya zimene inu 
Mumadya, ndi kumwa Zomwe inu 
mumamwa. 

34. Koma ngati mumvera 
Munthu wonga inu, Ndiye kuti 
mukhala otaika (oluza). 

35. Kodi akukulonjezani kuti 
mukadzafa Ndikusanduka dothi 
ndi mafupa, mudzaukitsidwanso 
(m'manda)? 

36. Sizingachitike, 
sizingachitike, zimene 
Mukulonj ezedwazi ! 

37. Palibe (moyo wina) koma 
moyo wathu Wapadzikowu basi! 
Tikufa ndiponso kukhala ndi 
moyo! Ndipo sitidzaukitsidwa 
M'manda. 

38. Uyu saali kanthu (amene 
akudzitcha Kuti ndi Mtumiki) 
koma ndi munthu basi, Akupekera 
Mulungu bodza, ndipo ife 

S itimkhulupir ira. " 

39. (Mtumikiyo) adati: "E, 
Mbuye wanga! Ndipulumutseni 
pakuti anditsutsa". 

40. (Mulungu) adati: 
"Posachedwapa akhala 
Odandaula." 

41. Choncho, mkuwe wa 
(chilango) choonadi 
Udawaononga, ndipo tidawachita 
Ngati zinyalala (zongotengedwa 






*$&&&#%&$& 

%£&&% 



%$.ofo$>Sic£> <M 



%j&&$&$s 






Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



728 



> A frji-l IT djsp 5jj~- 



ndi madzi). Choncho, kuonongeka 
kudatsimikizika Pa anthu 
osalungama. 

42. Ndipo titatero tidalenga 
mibadwo ina Pambuyo pawo. 

43. Palibe mtundu 
Ungafulumizitse kapena 
Kuichedwetsa nthawi yake yofera, 

44. Kenaka tidatuma atumiki 
Athu. Motsatizana; (wina pambuyo 
pa mnzake). Ndipo m'badwo 
uliwonse pamene adaufikira 
Mtumiki wake, udamtsutsa; ndipo 
Tidawaononga motsatana; ndipo 
tidawachita Kukhala nkhani (za 
anthu.) Ndipo kuonongeka 
Kudatsimikizika pa anthu 
osakhulupirira. 

45. Zitatero tidatuma Musa ndi 
m'bale wake Haaruna, pamodzi 
ndi zozizwitsa Zathu, ndi Umboni 
woonekera poyera, 

46. Kwa Farawo ndi nduna 
zake. Koma onse Adadzitukumula; 
ndipo adali anthu odzikweza. 

47.Ndipoadati:"Ha! 
Tikhulupirire anthu awiri Onga ife, 
omwe mtundu wawo ndi akapolo 
Athu!". 

48. Choncho adawatsutsa (onse 
awiri), ndipo Adali m'gulu la 
oonongedwa. 



qCZ&^M$&&8& 












Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



729 



>* ij±-\ rr o^jiiSj^ 



49. Ndipo ndithu, Musa 
Tidampatsa Buku kuti iwo 
Aongoke. 

50. Ndipo tidamchita mwana 
wa Mariamu ndi mayi wake 
kukhala Chisonyezo (choonetsa 
Kukhoza kwathu). Ndipo 
tidawapatsa malo Othawirapo, 
pachikweza, chokhazikika 
Pomwenso padali akasupe. 

51. E, inu Atumiki! Idyani 
Zakudya zabwino, Ndipo chitani 
zabwino. Ndithu, Ine ndi Wodziwa 
Zonse zimene muchita. 

52. (Tidauza mibadwo yawo): 
"Ndithu mpingo Wanuwu ndi 
mpingo umodzi, ndipo Ine Ndine 
Mbuye wanu; choncho ndiopeni". 

53. Koma adadula chinthu 
chawochi (Chipembedzo chawo) 
pakati pawo M'mipatukomipatuko; 
gulu lililonse Limasangalalira 
chimene lili nacho. 

54. Choncho, asiye mu umbuli 
wawo kufikira Nthawi (yakufa 
kwawo). 

55. Kodi akuganiza kuti 
Tikamawapatsa chuma Ndi ana, 

56. Tikuwafiilumizitsira 
zabwino. Sichoncho, koma Iwo 
sakuzindikira. 

57. Ndithu, amene amakhala 
amantha chifukwa Choopa Mbuye 



P®4$J&S&& 


















Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



730 



Sh *j*-l 



V T 0^j» jil 5jj~* 



wawo, (ndim'mene mathero Awo 
adzakhalire); 

58. Ndi omwe amakhulupirira 
aya za Mbuye Wawo; 

59. Ndi omwenso saphatikiza 
Mbuye wawo ndi Mafano; 

60. Ndi omwenso amapereka 
(zakaati ndi sadaka Kuchokera 
m'chuma) chimene apatsidwa, 
Uku mitima yawo ili yoopa kuti 
adzabwerera Kwa Mbuye wawo; 

61. Amenewa ndiamene 
akuchita changu Pa zinthu 
zabwino, ndipo iwo akutsogolera 
(Ena) pazimenezo. 

62. Ndipo sitikakamiza munthu, 
koma chimene Angathe 
(kuchichita). Ndipo tili naye 
Kaundula (wosunga chilichonse) 
yemwe Adzayankhula choonadi 
ndipo iwo Sadzaponderezedwa 

63. Koma mitima yawo ili 
Nkusalabadira mu ichi; Ndipo iwo 
ali ndi Ntchito zimene akuchita, 
Osati izi, 

64. Kufikira tikadzawaika 
m'chilango amene ali Opeza 
bwino, pompo adzakuwa 
(ndikupempha Chipulumutso). 

65. (Kudzanenedwa kwa iwo): 
"Musalire lero (Ndikupempha 
chipulumutso)! Ndithu, inu 
Simupulumutsidwa ndi Ife. 












%&9&&$m 



Surat 23. AI-Mu'minun Juzu 18 



731 



^A *>1 



Yf Uji^jll 3jj-*» 



66. "Ndipo aya Zanga 
zinkawerengedwa kwa Inu koma 
munkazibwezera kumbuyo 
Ndizidendene zanu, 

67. Uku mukudzikweza; 
Nkumakambirana usiku 
Zachabechabe zoinyoza (Qur'an)" 

68. Kodi sadaganizire liwu (ili 
limene wadza Nalo 
Mtumiki{SAW}), kapena 
zawadzera Zomwe 
sizidawadzerepo makolo awo 
Akale? 

69. Kodi kapena sadam'dziwe 
Mtumiki wawoyu (Makhalidwe 
ake) kotero kuti iwo Akum'kana? 

70. "Kapena akunena Kuti 
ngwamisala?" Koma Wawadzera 
ndi choonadi, Ndipo ambiri aiwo 
Amachida choonadi. 

71. Ndipo choonadi 
Chikadatsatira zofuna Zawo, ndiye 
kuti thambo Ndi nthaka ndi za 
m'menemo Zikadaonongeka! 
Koma Tawabweretsera 
chikumbutso chawo, koma Iwo 
akuchipewa chikumbutso 
chawocho. 

72. Kodi kapena ukuwapempha 
malipiro (Nchifukwa chake 
akuchikana Chipembedzochi)? 
Koma malipiro a Mbuye Wako 
ndiwo abwino; lye ndi Wopereka 
Wabwino kuposa opereka. 















%&J"p&jfi&- 






Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



732 



> A *ji-i Y T dji*£\ djj-- 



73. Ndipo ndithu, iwe 
ukuwaitanira kunjira Yolunjika; 
(supempha malipiro kwa iwo Pa 
kuitanako). 

74. Ndipo ndithu, amene 
sakhulupirira tsiku La chimaliziro, 
ali kutali ndi njira Ya choonadi. 

75. Ndipo tikadawachitira 
Chifundo ndi kuwachotsera 
Masautso omwe ali nawo, Ndithu, 
akadapitiriza Kuyumbayumba 
M'kuchita kwawo zoipa. 

76. Ndipo ndithu, Tidawalanga 
ndi chilango Chaukali, koma 
sadacheukire kwa Mbuye wawo 
ndikudzichepetsa, 

77. Kufikira pamene 
Tidawatsekulira khomo la 
Chilango chaukali; Pamenepo 
ndipo Adataya mtima. 

78. Ndipo lye ndi Yemwe 
adakupangirani Makutu, maso ndi 
moyo; Nzochepa zimene 
Mukuthokoza. 

79. Iyenso ndi Yemwe 
Wakufalitsani padziko;Kenako 
mudzasonkhanitsidwa kwa lye. 

80. Ndipo lye ndi Yemwe 
Amapatsa moyo ndi Imfa,ndipo 
kusinthana Kwa usiku ndi usana 
Nkwake. Kodi simuzindikira? 

81. Koma akunena monga 
(anthu) oyamba Adanenera. 



#iM^^ 


















0, 



K£B(W&*\$S& 



Surat 23. Al-MiTminun Juzu 18 733 I > A ^jJb-i Y r 0>^ jii 5jj-- 



82. Akunena: "Kodi tikadzafa 
ndikukhala Dothi ndi mafupa, 
tidzaukitsidwanso?" 

83. " Ndithudi ife ndi makolo 
athu kale Tidalonjezedwa zimenezi 
izi sikanthu koma Nkhambakamwa 
za anthu akale." 

84. Nena: "Kodi nthaka njayani 
ndi zomwe zili M'menemo, ngati 
inu Mukudziwa (kanthu)!" 

85. Adzanena kuti, "Nza 
Mulungu!" Nena: "Nanga bwanji 
simukumkumbukira(Kuti lye 
Ngokhoza chilichonse)? 

86. Nena: "Kodi ndani Mbuye 
wa thambo zisanu Ndi ziwiri, ndi 
Mbuye wa Mpando Waukulu?" 

87. Anena (kuti): "Nza 
Mulungu." Nena: "Nanga bwanji 
simukumuopa?" 

88. Nena: "Kodi ndani Yemwe 
m'manja Mwake Muli mphamvu 
yolamulira chinthu Chilichonse? 
Ndipo lye amateteza zonse. Ndipo 
palibe chimene Chingatetezedwe 
kuchilango Chake. Ngati inu 
mukudziwa." 

89. Anena (kuti): "Ndi 
Mulungu." Nena: "Nanga 
mukulodzedwa Bwanji (ndi satana)? 

90. Koma tawabweretsera 
choonadi; ndithu iwo Ngabodza 
(potsutsana ndi choonadicho). 









®G>$&n&&$% 






{j$\^ffity$\&&& 



® t 



®(yyW^I^V^w51fe - 






®(lJj^(J\9(^^i)t>pyi~' 



<^#£&V$&Ci 



Surat 23. Al-M u'minun Juzu 18 734 \A *>■» 



TV o^*jli 3j^» 



91. Mulungu sadadzipangire 
mwana, ndipo Padalibe pamodzi 
ndi lye mulungu (wina), Ngati 
zikadakhala choncho ndiye kuti 
mulungu Aliyense akadatenga 
zimene Adalenga, ndipo milungu 
ina ikadaipambana Milungu 
inzawo (polimbanirana ufumu) 
Mulungu wapatukana nazo 
kwambiri zimene Akusimbazo. 

92. Wodziwa zamseri ndi 
Zapoyera; watukuka Kuzimene 
akumphatikiza nazozo. 

93. Nena: "E, Mbuye wanga! 
Ngati mungandionetse zomwe 
Akulonjezedwa (ndikadali ndi 
moyo), 

94. E, Mbuye wanga! 
Musandikhazike M'gulu la anthu 
osalungama". 

95. Ndipo ndithu, Ife 
ndiWokhoza kukuonetsa 
(Chilango) chimene Tikuwalonjeza. 

96. Chotsa zoipa (zimene 
akukuchitira) Powabwezera 
zabwino; Ife tikudziwa Zimene 
akunena. 

97. Ndipo nena: "E, Mbuye 
wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi inu 
Kumanong'onong'o a satana. 

98. "Ndiponso 
ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye 
Wanga kuti asandidzere." 






v$z&&^& 



t '9%> V 






*$\4&^&C 



JL 












®, 






Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



735 



\ A * ji-l V T djv>£\ Ojj~* 



99. Kufikira m'modzi wawo 
ikam'dzera imfa, Amanena: 
"Mbuye wanga! Ndibwezereni (Ku 
moyo wa padziko), 

100. Kuti ndikachite zabwino 
pazimene Ndidasiya." (Angelo 
amayankha kuti): "Iyayi! Ndithu, 
awa ndi mawu basi Amene iye 
akulankhula (imfa Ikamfika)." 
Ndipo patsogolo pawo Pali 
chiyembekezo; (moyo 
Wamasautso kwa oipa; ndipo 
wamtendere Kwa abwino) kufikira 
tsiku limene Adzaukitsidwa. 

101. Choncho, lipenga 
likadzaimbidwa, Sipadzakhala 
chibale Pakati pawo tsiku 
Limenelo, ndipo Sadzafunsana. 

102. Tsono omwe mlingo (wa 
zochita zawo Zabwino) 
udzalemere, iwowo ndiwo 
Opambana, 

103. Ndipo omwe miyeso yawo 
(yazochita Zabwino) idzatsike, 
iwowo ndi omwe Adadziluzitsa 
okha; adzakhala ku Jahannama 
Muyaya . 

104. Moto ukawawula nkhope 
zawo, ndipo Adzakhala m'menemo 
Uku akukukuta (mano). 

105. (Adzauzidwa): "Kodi aya 
Zanga Sizidali kuwerengedwa kwa 
inu ndipo inu Nkumazitsutsa?" 



%20 


















Surat 23. Al-Mu'minun Juzu 18 



736 



\ A * j£-l Y T O^i* jil 5 j j-j 



106. Adzati: "Mbuye wathu! 
Zoipa zathu Zidatigonjetsa, 
choncho tidali anthu Osokera. 

107. Mbuye wathu! Titulutseni 
umu (M'moto ndikutibwezera 
kudziko lapansi Kuti tikachite 
ntchito yabwino); Ngati 
titabwerezanso kuchita zoipa, 
Ndiye kuti tidzakhaladi oipa 
Odziononga tokha." 

108. (Mulungu) adzati: 
"Khalani chete m'menemo, 
Monyozeka! Ndipo 
musandilankhule ! 

109. Ndithu, mwa akapolo anga 
lidalipo gulu Lomwe linkanena: 
"Mbuye wathu! Takhulupirira; 
choncho tikhululukireni 
Ndikutichitira chifundo; ndipo inu 
Ngabwino kwambiri kuposa (ena 
onse) Ochita chifundo." 

110. "Koma inu mudawachita 
Chipongwe kufikira 
Adakuiwalitsani kundikumbuka 
Uku muli kuwaseka." 

111. "Ndithu, Inelero 
ndawalipira (munda Wa mtendere) 
chifukwa cha kupirira Kwawo; 
ndithu, iwo ndiwo opambana." 

112. Adzanena: "Kodi 
mudakhala Nthawi yotani padziko 
Pachiwerengero cha zaka?" 



*^^<s»®gfts 



©I 



x **f^ \49<* 






ty&Sty&MZ 






©u£$$j3t 



Surat 23. AI-MiTminun Juzu 18 



737 > A frj£-l XT Opjil 5jj*. 



113. Adzayankha: "Tidakhala 
tsiku limodzi Kapena gawo la 
tsiku; (adzatero poyerekeza 
Ndikutalika kwa moyo 
wamasautso kumoto); Afunse 
owerengera." 

114. Adzanena: "Inu 
simudakhale (kudzikoko) Koma 
pang'ono basi, mukadakhala 
Mukudziwa (chilango chomwe 
Chakufikanichi, sibwenzi 
mukuchita zoipa). 

115. "Kodi mumaganiza Kuti 
tidakulengani chabe, Ndikuti 
simdzabwezedwa kwa Ife?" 

116. Watukuka Mulungu, 
Mfumu ya Choonadi; palibe 
wompembedza Mwachoonadi 
koma lye, Bwana Wa Mpando 
Wolemekezeka (Kwambiri).' 

117. Ndipo amene apembedza 
mulungu wina Pomphatikiza ndi 
Mulungu (weniweni), 
Chikhalirecho iye alibe umboni 
Pazimenezo; basi chiwerengero 
chake Chili kwa Mbuye wake. 
Ndithu, Osakhulupirira 
sangapambane. 

118. Choncho nena: "Mbuye 
wanga! Ndikhululukireni 
ndikundichitira Chifundo! Inu 
Ngabwino kuposa achifundo." 


















Surat 24. An-Niir Juzu 18 



738 



1A ftji-1 



1 1 jjJl ^JJ- - 




Msurayi Mulungu wafotokoza zakufunika koyeretsa mtundu 
kumachitidwe a chiwerewere. Ndipo surayi ikuletsa kufalitsa 
zoipa pakati pa Asilamu, ndikukhazikitsa zilango kwa anthu kuti 
machitidwewa alekeke. Ndipo yafotokozanso miyambo 
yokhalirana pakati pa Asilamu pamoyo wawo -monga kuodika 
polowa mnyumba, ndikuzolitsa maso, ndikusunga umaliseche. 
Ndiponso kuti amuna ndi akazi amene sali anyazi, 
asamasanganikirane . 

Surayi yafotokozanso zofunika pabanja la chisilamu-monga 
kudzipatsa ulemu, kudziyeretsa kumachitidwe osayenera 
ndikukhala wolungama nthawi zonse. 




Surat 24. An-Nur Juzu 18 



739 



^A *>i 



1 i jjJt Oj^- 



SuratAl-NurXXIV 









M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Iyi ndi sura; Taivumbulutsa, 
ndipo Taikamo Malamulo. Ndipo 
m'menemo Tatumizamo aya 
zomveka kuti Mukumbukire 
(malamulo ndi Kuchita nawo 
m'njira Yoyenera). 

2. Mkazi wachiwerewere ndi 
mwamuna wa Chiwerewere 
aliyense wa iwo mkwapuleni 
Zikoti zana limodzi (100). 
Musagwidwe chisoni ndi iwo pa 
Chipembedzo (malamulo) cha 
Mulungu, ngati inu 
mukukhulupiriradi Mwa Mulungu 
ndi tsiku la chimaliziro. Ndipo 
gulu la Asilamu lionerere Chilango 
cha iwo. 

3. Mwamuna wa chiwerewere 
sakwatirana Ndi mkazi (wabwino) 
koma Wachiwerewere mnzake, 
kapena mkazi Wopembedza 
mafano. Nayenso mkazi 
Wachiwerewere sakwatirana ndi 
Mwamuna (wabwino) koma 
wachiwerewere Mnzake, kapena 
wopembedza mafano. Ndipo 
zimenezi zaletsedwa kwa Asilamu. 

4. Ndipo amene akunamizira 
akazi Odziteteza (powanamizira 



o^l^jll^U. 



-a 















W^*UisJJb 



Surat 24. An-Nur Juzu 18 



740 I > A *>i 



1 1 j>Jl 5j^ 



kuti Achita chiwerewere), ndipo 
osabwera nazo Mboni zinayi, 
akwapuleni zikoti 80; Ndiponso 
musauvomereze umboni wawo 
Mpaka kalekale. Iwo ngotuluka 
M'chilamulo cha Mulungu, 

5. Kupatula amene alapa 
pambuyo Pazimenezo, ndipo 
nkukonza (zochita Zawo), Ndithu, 
Mulungu Ngokhululuka; 
Ngwachisoni, (awakhululukira). 

6. Ndipo amene akunamizira 
akazi awo (kuti achita 
chiwerewere) ndipo Iwo nkukhala 
opanda mboni, koma (Iwo) okha, 
choncho umboni Wa mmodzi wa 
iwo (umene Ungamchotsere 
chilango chomenyedwa Zikoti 80), 
ndikupereka umboni Kanayi 
polumbirira Mulungu kuti ndithu, 
lye ndi mmodzi mwa onena zoona; 

7. Ndipo kachisanu (alumbire) 
kuti Matemberero a Mulungu 
akhale pa iye Ngati (iye) ali 
m'modzi mwa onama. 

8. Ndipo (mkazi) chilango 
amchotsera Atapereka umboni 
kanayi polumbirira Mulungu kuti 
(uyu mwamuna) ndi mmodzi mwa 
onama. 

9. Ndipo kachisanu (alumbire) 
kuti Mkwiyo wa Mulungu ukhale 
pa iye Ngati (mwamuna wake) ali 
mmodzi Mwa onena zoona. 






&{£ IV* 









3BteWy>^6foJ*K 



"safe 









Q)f>- \ U ' 



(&,^(y*. 



Surat24. An-Nur Juzu 18 I 741 I > A *>H 



T £ jjJl $jj-*> 



10. Ndipo pakadapanda ubwino 
wa Mulungu ndi Chifundo chake 
pa inu (mukadavutika). Ndipo 
Ndithu, Mulungu Ngolandira 
kulapa; . Wanzeru zakuya. 

11. Ndithu, amene adza ndi 
bodza (Ponamizira Mayi Aisha, 
yemwe ndi Mkazi wa Mtumiki, 
kuti wachita Chiwerewere), ndi 
gulu la mwa inu. Musaganizire 
zimenezo kuti nzoipa Kwa inu, 
koma kuti zimenezo nzabwino 
Kwa inu. Ndipo munthu aliyense 
Waiwo apeza (chilango) 
pamachimo Amene wawachitawo. 
Ndipo yemwe Wasenza gawo 
lalikulu lauchimowo Mwa iwo, 
adzapeza chilango chachikulu 

12. Nanga bwanji pamene 
Mudaimva (nkhani) Iyi Asilamu 
achimuna Ndi Asilamu achikazi 
Sadaganizire anzawo zabwino 
Ndikunena kuti: "Hi ndi bodza 
loonekera?" 

13. Nanga bwanji sadabweretse 
mboni Zinayi (pazimenezi)? Ndipo 
pamene Alephera kubweretsa 
mboni, iwo Ngabodza kwa 
Mulungu. 

14. Ndipo pakadapanda ubwino 
wa Mulungu Ndi chifundo chake 
pa inu, padziko Lapansi ndi 
patsiku lachimaliziro, Chilango 
chachikulu chikadakukhudzani Pa 
zomwe munkazijijirikira. 



%\8^$sw&8& 



fiW^&f 















Siirat 24. An-Nur Juzu 18 



742 |1A »>i 



Y t jy i\ oj^ 



15. Pamene mudalilandira 
(bodzalo) ndi Malirime anu ndi 
kumanena ndi milomo Yanu 
zomwe inu simukuzidziwa, ndipo 
Mumaganizira kuti ndi chinthu 
Chochepa pomwe icho kwa 
Mulungu Ndi chinthu chachikulu. 

16. Ndipo nanga bwanji pamene 
mudalimva (Bodzalo) simudanene 
(kuti): "Sikoyenera kwa ife 
kulankhula izi; Kuyera nkwanu 
(Mbuye wathu). Hi Ndi bodza 
lalikulu." 

17. Mulungu akukulangizani 
kuti: "Musabwerezenso kuchita 
zonga Zimenezi mpaka kalekale, 
ngati inu Muli okhulupirira 
enieni." 

18. Ndipo Mulungu 
akukufotokozerani Aya Zake 
mwatsatanetsatane. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa; Ngwanzeru 
zakuya. 

19. Ndithu, amene akukonda 
kuti Zoipa zifale pa amene 
akhulupirira, Chilango chowawa 
chili pa iwo Padziko lapansi ndi 
patsiku la Chimaliziro. Ndipo 
Mulungu ndi Yemwe akudziwa 
(zoyenerana ndi Inu), koma inu 
simudziwa. 

20. Ndipo pakapanda ubwino 
wa Mulungu Ndi chifundo chake 
pa inu, (Pakadapezeka zauve). 






efcr 









4&&ti£M®W& 






wz®%g&M&& 






Surat 24. An-Nur Juzu 18 



743 



>A tf-jA-i 



t £ j>Ji 5j>- 



Koma ndithu, Mulungu Ngofatsa; 
Ngwachifundo. 

21. E, inu amene 
mwakhulupirira, Musatsatire 
mapazi a satana. Ndipo amene 
atsatire Mapazi a satana (asokera) 
ndithudi lye akulamula zauve ndi 
zoipa. Ndipo Pakapanda ubwino 
wa Mulungu ndi Chifundo chake 
pa inu, sakadayera Aliyense mwa 
inu mpaka kalekale. Koma 
Mulungu amamuyeretsa amene 
wamfuna. Ndipo Mulungu 
Ngwakumva zonse; Wodziwa 
kwambiri. 

22. Ndipo ochita zabwino 
(padziko Lapansi), ndiponso eni 
kupeza Bwino mwa inu, 
asalumbire kuti Aleka kupatsa 
achinansi, Masikini, ndi osamuka 
panjira Ya Mulungu. Koma 
Akhululuke Ndikuleka zimenezo. 
Kodi Simufuna kuti Mulungu 
Akukhululukireni? Mulungu 
Ngokhululuka 

kwambiri .Ngwachisoni (Choncho, 
nanunso teroni). 

23. Ndithu, amene akunamizira 
akazi Oyera (kumachitidwe 
Achiwerewere), odziteteza 
Kumachitidwe oipa, okhulupirira, 
Atembereredwa padziko lapansi 
ndi Patsiku la chimaliziro. Ndipo; 
Chilango chachikulu chili pa iwo; 












Surat 24. An-Nur Juzu 18 



744 h A *j*-> 



Y i jjJt Sjj-*> 



24. Tsiku lomwe malirime awo, 
mikono Yawo ndi miyendo yawo 
zidzawachitira Umboni pazomwe 
adali kuchita. 

25. Tsiku limenelo Mulungu 
Adzawapatsa mphotho yawo ya 
choonadi, Ndipo adzadziwa kuti 
Mulungu ndiye Mwini kulipira 
kwachoonadi Koonekera poyera. 

26. Akazi oipa ndi Aamuna 
oipa, naonso Amuna oipa ndi 
aakazi Oipa; ndipo akazi abwino 
Ndi aamuna abwino, Naonso 
amuna abwino ngaakazi abwino. 
Iwowa ngopatulidwa kuzimene 
akunenazo. I wo adzapeza 
chikhululuko ndi riziki Laulemu 
(ku Munda wa Mtendere). 

27. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musalowe 
m'nyumba zomwe Sinyumba zanu 
kufikira mutapempha Chilolezo 
poodira ndikupereka Salaamu kwa 
eni nyumbazo. Kutero ndi kwa 
Bwino kwa inu kuti mukumbukire 
(Nkuona kuti zomwe mukuuzidwa 
Nzabwino). 

28. Koma ngati simupeza 
munthu aliyense M'menemo, 
musalowe kufikira Mutapatsidwa 
chilolezo. Ndipo Mukauzidwa 
kuti: "Bwererani, Bwererani; 
chimenechi nchokuyeretsani. 
Ndipo Mulungu akudziwa Zimene 
muchita. 









% 









Sfirat 24. An-Nur Juzu 18 



745 



>A *>» 



T t jjA\ t^ 



29. Sikulakwa kwa inu kulowa 
m'nyumba Zosakhalidwa, (monga 
sitolo, hotela; Popanda chilolezo), 
momwe muli Zokuthandizani; 
ndipo Mulungu Akudziwa zomwe 
mukuonetsera poyera Ndi zimene 
mukubisa. 

30. Auze Asilamu achimuna 
kuti adzolitse Maso awo 
(asayang'ane zoletsedwa), Ndipo 
asunge umaliseche wawo. Ichi 
Nchoyera kwambiri kwa iwo. 
Ndithu, Mulungu akudziwa nkhani 
za zonse Zomwe achita. 

31. Ndipo auze Asilamu 
achikazi kuti adzolitse Maso awo, 
ndikusunga umaliseche wawo, 
Ndipo asaonetse (poyera) zomwe 
Amadzikongoletsa nazo kupatula 
zimene Zaonekera poyera 
(popanda cholinga Chotero). 
Ndipo afunde kumutu mipango 
Yawo mpaka m'zifuwa zawo; 
ndipo asaonetse Poyera 
zodzikongoletsa nazo koma kwa 
Amuna awo, kapena atate awo, 
kapena Apongozi awo, kapena ana 
awo, kapena ana A amuna awo, 
kapena abale awo, kapena ana A 
abale awo, kapena ana a alongo 
awo, Kapena akazi anzawo 
(achisilamu). Kapena Yemwe 
wapatidwa ndi dzanja lamanja 
(Monga kapolo), kapena otsatira 
(antchito) Omwe ndi amuna 















Surat 24. An-Nur Juzu 18 



746 



^A frjJUi 



Y t j>3» 5j>* 



opanda zilakolako za akazi Ndi 
ana omwe sadziwa za ukazi. Ndipo 
Asamenyetse miyendo yawo 
(pansi) kuti Zidziwike zimene 
akubisa mwa zomwe 
Amadzikongoletsa nazo. 
Tembenukirani Kwa Mulungu, 
nonse inu okhulupirira Kuti 
mupambane. 

32. Ndipo zikwatitseni mbeta za 
mwa inu (mfulu), Ndi akapolo anu 
amene ali abwino (achimuna) Ndi 
adzakazi anu. Ngati ali osauka 
Mulungu Awalemeza kuchokera 
m'zabwino Zake. Ndipo Mulungu 
za ufulu Zake nzambiri (Zopanda 
muyeso,ndiponso), Ngodziwa 
Kwabasi. 

33. Ndipo amene sapeza 
chokwatirira Apewe (uve wa 
chiwerewere) kufikira Mulungu 
atawalemeza ndi zabwino Zake. 
Ndipo amene afuna kuti 
awalembere (kuti Apate ufulu) 
mwa amene Manja anu akumanja 
apeza, alembereni (Kuti 
adziombole). Ngati mwaona 
Zabwino mwa iwo apatseni gawo 
La chuma cha Mulungu chomwe 
akupatsani. Musawakakamize 
adzakadzi anu kuchita uhule Ngati 
akufuna kudzisunga, ncholinga 
choti Mupeze zinthu zamoyo 
wadziko lapansi. Ndipo amene 
angawakakamize, ndithu Mulungu, 









Surat 24. An-Nur Juzu 18 



747 



>A *>» 



Y t j>Jt ojj^ 



pambuyo Pokakamizidwa 
kwawoko, Ngokhululuka; 
Ngwachisoni (Kwa 
okakamizidwawo) . 

34. Ndipo ndithu,tatumiza Kwa 
inu aya zofotokoza (Zofunika 
zonse) mwatsatanetsatane, Ndi 
mafanizo (okuphanulani maso) Pa 
za amene adamuka patsogolo 
panu, Ndi phunziro kwa oopa 
(Mulungu). 

35. Mulungu nkuunika kwa 
kuthambo ndi Nthaka. Fanizo la 
kuunika kwake (Powaongolera 
akapolo ake) lili ngati "Mishikati" 
(chibowo cha pa khoma choikapo 
Nyali) yomwe mkati mwake 
mwaikidwa nyali. Nyali ili 
m'galasi. Ndipo galasilo lili ngati 
Nyenyezi yowala.Nyali imeneyo 
imayatsidwa Ndi mafuta ochokera 
kumtengo wodalitsidwa Wa 
mzitona, womwe suli mbali 
yakuvuma Ngakhale kuzambwe; 
(umamenyedwa Kwambiri ndi 
dzuwa pamene likutuluka, Ndi 
pamene likulowa.) Mafuta ake 
Ngoyandikira kukuwala okha 
(chifukwa Champhamvu yake), 
ngakhale moto Usanawakhudze. 
Kuunika pamwamba pa Kuunika! 
Mulungu amamuongolera kuunika 
Kwake amene wamfuna. Mulungu 
amaponya Mafanizo kwa anthu 
(kuti aganizire ndi Kupeza 



6®W 



}&2J £*• 1>*& <&^j£ 



Surat 24. An-Nur Juzu 18 



748 



>A *>l 



T £ jj-Ji Sj^-" 



phunziro) Mulungu ngodziwa 
Chilichonse. 

36. (Apezeke akupemphera 
kasanu) m'nyumba Zomwe 
Mulungu walamula kuti 
Zilemekezedwe; ndipo M'menemo 
dzina Lake Litchulidwe; 
azimulemekeza m'menemo 
(M'misikiti) kum'mawa ndi 
kumadzulo; 

37. Anthu omwe malonda 
Ogulitsa ndi kugula 
Sawatangwanitsa posiya 
Kukumbukira Mulungu ndi 
Kupemphera (swala) ndi kupereka 
Chopereka (zakaat). Amaopa tsiku 
lomwe Mitima ndi maso 
zidzasinthika; 

38. Kuti Mulungu adzawalipire 
Zabwino pa zomwe Adachita ndi 
kuwaonjezera Zabwino Zake. 
Ndipo Mulungu Amampatsa 
amene wamfuna Popanda 
chiwerengero. 

39. Ndipo amene 
sadakhulupirire, ntchito zawo 
(Zimene akuziona ngati zabwino) 
zidzakhala Ngati zideruderu 
m'chipululu chamchenga; 
Waludzu nkumaganizira kuti 
ndimadzi; ndipo Akapita 
pamenepo, osaonapo chilichonse. 
(Nawonso pomwe adzadza 
kuzochita zawo Zabwino patsiku la 



V*if ^^"A^ 9 \k 



TO^^3&6fe& 



'&':'l\$X'\tf>"!'> 



P&ir**. 












Surat 24. An-Nur Juzu 18 



749 



1A *j£-i 



T £ jj-y' *jj-" 



Kiyama sadzapeza Mphotho 
iliyonse, chifukwa chakuti 
Adachimenya nkhondo 
Chisilamu). Ndipo Adzapeza 
Mulungu kumeneko, ndipo 
Adzamkwaniritsira chiwerengero 
chake Ndipo Mulungu 
Ngwachangu Powerengera. 

40. Kapena (ntchito zawo 
zoipazo) zili ngati M'dima mkati 
mwanyanja yamadzi ochuluka 
Yomwe yaphimbidwa ndi 
mafunde, ndipo Pamwamba 
pamafundewo pali mafundenso. 
Ndiponso pamwamba pake 
(mafundewo) Pali mitambo.Ndipo 
m'dima uwu pamwamba Pa 
m'dima uwu. Ndipo akatulutsa 
mkono Wake, sangathe kuuona 
(chifukwa Chakuchindikala kwa 
m'dima). Ndipo amene Mulungu 
sadampatse kuunika, sakhala nako 
Kuunika. 

41. Kodi suona kuti zonse 
zopezeka kumwamba Ndi pansi 
zikumulemekeza Mulungu, 
kudzanso Mbalame zikatambasula 
mapiko awo (Ngakhalenso 
zikapanda kutambasula) 
Chilichonse (mwazimenezo) 
chikudziwa Pemphero lake ndi 
m'mene Chingamulemekezere 
(Mulungu wake). Ndipo Mulungu 
Ngodziwa Zonse zimene akuchita. 









Surat 24. An-Nur Juzu 18 



750 I > A «-j*-i 



y t jy }\ ij^ 



42. Ufumu wakumwamba ndi 
pansi, ngwa Mulungu (yekha); 
ndipo kobwerera kwa Zonse nkwa 
Mulungu. 

43. Kodi suona kuti Mulungu 
akuyendetsa Mitambo, kenako 
nkuikumanitsa pamodzi, Ndipo 
kenako nkuikhazika m'milumilu? 
Nuona mvula ikutuluka pakati pa 
iyo. lye Akutsitsa mapiri 
amitambo kuchokera Kumwamba 
momwe muli mvula yamatalala; 
Ndipo amamenya nawo Amene 
wamfuna, ndikumpewetsa Amene 
wamfuna. Kung'anima kwake 
Kumayandikira kuchititsa Khungu. 

44. Mulungu amasintha usiku 
ndi usana (Pambuyo pa usiku, 
umadza usana. Ndipo pambuyo pa 
usana, umadza usiku). Ndithu, 
m'zimenezo muli phunziro kwa 
Anthu ozindikira (zinthu). 

45. Ndipo Mulungu adalenga 
ndi madzi nyama Iliyonse; (madzi 
ndicho chiyambi cha Zolengedwa 
zonse). Zina mwa izo Zimayendera 
mimba zawo; ndipo zina Mwa izo 
zimayenda ndi miyendo iwiri; 
Ndipo zina mwaizo zimayenda ndi 
inayi. Ndithu Mulungu amalenga 
chimene Wafuna; ndithu, Mulungu 
ali ndi Mphamvu pachilichonse. 

46. Ndithu, tavumbulutsa Aya 
zofotokoza Momveka (chilichonse 
chofunika pa Chipembedzo). 






4a* 






y 



t&ty&ftK3$to<& 



®j 






9 * 9 9'J\ { Sh \«'£ ^&\'K*<A 



Surat 24. An-Nur Juzu 18 



751 



^A *->! 



Y t j>J» *jj~> 



Ndipo Mulungu Amamuongolera 
kunjira yolunjika amene Wamfuna. 

47. Ndipo akunena (kuti): 
"Takhulupirira Mulungu Ndi 
Mtumiki, ndipo tamvera." Kenako 
ena a iwo amatembenuka Pambuyo 
pazimenezo; Ndipo iwo wo sali 
okhulupirira. 

48. Ndipo akawaitanira kwa 
Mulungu ndi Mtumiki wake kuti 
awaweruze pakati pawo, Ena a iwo 
akukana zimenezo 
(Akadzizindikira okha kuti 
ngolakwa) 

49. Koma akaona kuti 
chilungamo chili kwa iwo? Iwo, 
amam'dzera (Mtumiki 
mwachangu) Uku akusonyeza 
kumvera. 

50. Kodi ali ndi matenda 
m'mitima mwawo? Kapena 
akukaika, kapena akuopa kuti 
Mulungu ndi Mtumiki Wake 
awachitira Chinyengo? Koma iwo 
ndi amene ali Osalungama. 

51. Ndithu yankho la Asilamu 
akaitanidwa kwa Mulungu ndi 
Mtumiki Wake kuti aweruze pakati 
pawo Silikhala lina koma kunena 
Kuti: "Tamva ndipo titsatira." 
Iwowo ndiwo Opambana. 

52. Ndipo amene amvera 
Mulungu ndi Mtumiki Wake, 
ndikumalemekeza Mulungu ndi 



k 9'< 9 * ?99* &9 { V<"'l. 






^'^m.m&& 






iH »< »9'9* ,&9'\.\ 99" 






Surat 24. An-Nur Juzu 18 



752 



^A *j*-1 



V t j_jJl 5jj-»> 



kumuopa, Iwowo ndiwo 
opambana. 

53. Ndipo akulumbirira dzina la 
Mulungu, kulumbira Kwakukulu 
kuti ukawalamula (kupita 
Kunkhondo), ndithu apita. Nena: 
"Musalumbire; kumvera kwanu 
nkodziwika (Kuti nkwabodza); 
ndithu, Mulungu Akudziwa nkhani 
zonse zomwe muchita. 

54. Nena: "Mverani Mulungu, 
ndiponso Mverani Mtumiki. Koma 
ngati mutembenuka, lye ali nazo 
zimene wasenzetsedwa (kuti 
Azifikitse kwa inu), (ndipo) inunso 
muli nazo Zimene 

m wasenzetsedwa (kuti muzitsate). 
Ndipo mukamumvera, muongoka. 
Ndipo Pa Mtumiki palibe china 
chake koma Kufikitsa (uthenga) 
moonekera. 

55. Mulungu walonjeza mwa 
inu amene Akhulupirira ndikuchita 
ntchito yabwino kuti Ndithu 
awathandiza kukhala oyang'anira 
Padziko monga momwe 
adawachitira amene Adalipo kale 
kukhala oyang'anira; Ndipo 
ndithu, awalimbikitsira 
chipembedzo Chawo chimene 
wawayanja nacho; ndipo 
Awachotsera mantha awo kukhala 
opanda Mantha". Akhale 
akundirambira Ine, 
Osandiphatikiza ndi chilichonse. 






© 



f?\' 9 &'te m.\f. 



}"**>••* 



at& 









Surat 24. An-Nur Juzu 18 



753 



^A *jA-i 



Y t j^Ji 3^ 



Ndipo Amene asiye kukhulupirira 
pambuyo Pazimenezi, iwo 
ngakuswa malamulo. 

56. Choncho, pempherani swala 
ndi kupereka "Zakaat;" ndiponso 
mverani Mtumiki Kuti 
mumveredwe chisoni. 

57. Amene sadakhulupirire 
musawaganizire Kuti 
angamulepheretse Mulungu 
padziko (kuwalanga) ndipo Malo 
awo ndi kumoto. Ha! Kuipa Malo 
obwererako! 

58. E, inu amene 
mwakhulupirira! Akuodireni 
Amene manja ami akumanja apeza 
ndi amene Mwa inu sanathe 
msinkhu awodire nthawi zitatu: 
Isanapempheredwe swala ya 
m'mawa, Ndi pamene mukuvula 
nsalu zanu nthawi Yamasana (kuti 
mupumule), ndi pambuyo Pa swala 
ya Isha (usiku). Izi ndi nthawi 
Zitatu zomwe Inu mumakhala 
wamba. Palibe Uchimo pa inu 
ngakhale pa iwo pambuyo Pa 
nthawi zimenezo (kulowa popanda 
kuodira); Mumazungulirana pakati 
Panu umo ndi momwe 
Akukufotokodzerani Mulungu Aya 
zake. Ndipo Mulungu Ngodziwa; 
Ngwanzeru zakuya. 

59. Ndipo mwainu ana akatha 
msinkhu, aodire Monga momwe 
adali kuodira omwe adalipo 



\^&&1&W& 



%ggfri'\»'4\ 






m?> ' ?\'& '&g "fry*. _ .» >? 






® 



A'vt '. >\ 






SO rat 24. An-Nur Juzu 18 



754 



^A frjA-i 



1 1 jjJi ^j^ 



Patsogolo pawo. Umo ndi momwe 
Mulungu Akukufotokozerani aya 
Zake. Ndipo Mulungu Ngodziwa; 
Ngwanzeru zakuya; 

60. Nayonso mikwezembe 
(nkhalamba Zachikhalire zazikazi) 
Yomwe siyembekezera 
kukwatiwa, Palibe uchimo paiyo 
kusiya Kufunda nsalu zawo 
(kumutu), popanda Kuonetsa 
zodzikongoletsera zawo. Koma 
ngati zikudzikakamiza kuleka 
Kuvula mipangoyo, ndibwino kwa 
iyo. Ndithu, Mulungu 
Ngwakumva; Ngodziwa. 

61. Palibe kulakwa pa akhungu 
(osapenya) Ndiponso palibe 
kulakwa pa olumala; Palibenso 
kulakwa pa odwala, Ngakhalenso 
pa inu eni ngati muli kudya 
M'nyumba zanu kapena 
m'nyumba za atate Anu, kapena 
m'nyumba za amayi anu, Kapena 
m'nyumba za abale anu, kapena 
M'nyumba za alongo anu, kapena 
M'nyumba za abambo anu 
aang'ono kapena Aakulu, kapena 
m'nyumba za azakhali anu, 
Kapena m'nyumba za atsibweni 
anu, kapena M'nyumba za amayi 
anu aakulu kapena Aang'ono, 
kapena m'nyumba za omwe 
Mukuwasungira makiyi, kapena 
(m'nyumba Za) anzanu; palibe 
kulakwa pa inu ngati Mukudyera 



h "'3?*l * ' * * 9 ~ 9 <> 9 Yki " . 









Siirat 24. An-Niir Juzu 18 



755 



1A *>i 



Y £ j>Jl 5jj-< 



limodzi kapena payekhapayekha. 
Ndipo mukamalowa m'nyumba 
Dziperekereni nokha salaamu. 
(Lonjero ili) Ndi malonje ochokera 
kwa Mulungu Amadalitso, abwino. 
Umo ndi momwe Mulungu 
akukulongosolerani aya Zake kuti 
Muzindikire. 

62. Ndithu, Asilamu oona 
ndiamene Akhulupirira mwa 
Mulungu ndi Mtumiki Wake; 
ndipo akakhala naye pachinthu 
Chokhudza onse, sachoka mpaka 
Atampempha (Mtumiki) chilolezo. 
Ndithu, amene akukupempha 
chilolezo, Iwowo ndi amene 
akukhulupirira Mulungu ndi 
Mtumiki Wake. Choncho 
akakupempha chilolezo Chifukwa 
cha zinthu zawo zina, Muloleze 
mwaiwo amene wamfuna (ngati 
Utaona kuti chidandaulo chake 
Nchoona), ndipo uwapemphere 
Chikhululuko kwa Mulungu; 
ndithu, Mulungu Ngokhululuka 
kwabasi; Ngwachisoni 

63. Kumuitana Mtumiki pakati 
panu Musakuchite monga momwe 
Mumaitanirana nokhanokha, 
ndithu, Mulungu akudziwa amene 
akuchoka Pamalo mozemba ndi 
modzibisa mwa inu. Achenjere 
amene akunyozera lamulo Lake 
kuti mliri Ungawapeze, kapena 
Kuwapeza chilango chowawa. 



&&&*$& 









Surat 24. An-Nur Juzu 18 I 756 I \ A *j*-i 



T i jjJl ^jj-** 



64. Mverani! Ndithu, zili 
kumwamba ndi Pansi nzake 
Mulungu ndipo akudziwa Zimene 
muli nazo. Ndipo patsiku Limene 
adzabwezedwe kwa lye, 
Adzawaudza zimene adachita 
ndipo Mulungu Ngodziwa 
chilichonse. 







Surat 25. Al-Furqan Juzu 18 757 1 A *>i to aiS^di 3jj~- 




Surayi yayamba ndi kufotokoza zaulemerero wa Qur'an, ndi 
kuphanuka kwa ufumu wa Yemwe adaivumbulutsa; Yemwe 
ufumu wakumwamba ndi pansi Ngwake. 

Koma ngakhale ufumu Wake uli waukulu chonchi, 
Amshirikina akumphatikiza ndi milungu ina pomwe lye ndi 
mmodzi ndipo palibe wachiwiri wake, iwo akutsutsa Qur'an 
pamodzi ndi uthenga wa Mtumiki Muhammad (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) pomunena kuti angakhale Mthenga wa 
Mulungu bwanji pomwe ali munthu; amadya chakudya 
ndikumapita kumisika monga anthu ena. ndipo Amshirikina 
akufuna kuti Mthengayo koma akadakhala mmodzi wa angelo. 
Ndipo akuyankhidwa kuti Mulungu akadatuma mngelo monga 
Mtumiki, ndiye kuti mngeloyo akadamsandutsa maonekedwe 
ndi chikhalidwe chake kukhala monga anthu kuti amvane bwino 
ndi anthu wo. 

Amshirikina adatsutsa kuti kodi bwanji Qur'an 
idavumbulutsidwa pang'onopang'ono, osati mwa nthawi imodzi 
monga momwe zidalili ndi mabuku ena? Ndipo adawayankha 
kuti zidachitika zimenezi ndi cholinga chanzeru zakuya. 

Qur'an idapitiriza kuwafotokozera zomwe zidachitikira 
Aneneri akale ndi anthu awo kuti likhale phunziro kwa iwo. 
Koma Amshirikina sadacheukire zimenezi, adangotsatira 
zilakolako zawo basi. Potero, adasokera ngati nyama kapenanso 
kuposa nyama. 

Tsono surayi yasonyeza zisonyezo zachilengedwe zomwe 
zikuonetsa mphamvu za Mulungu. Ndipo surayi yamaliza ndi 
kufotokoza mbiri za okhulupirira zomwe zikaalowetse anthuwo 
ku Janna, m'minda ya mtendere momwe azikalandira malonje 
abwino. 



Surat 25. Al-Furqan Juzu 18 758 >A tji-i 



T o JlSyJl 5 jj-o 



Surat Al-Furqan XXV 



_j^ 



mmZ 



M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Watukuka Mwini kupereka 
madalitso, Yemwe Wavumbulutsa 
Qur'an kwa kapolo Wake kuti 
Ikhale mchenjezi kwa zolengedwa 
zonse. 

2. (Mulungu) Yemwe Ngwake 
ufumu Wakumwamba ndi 
wapansi. Ndipo Sadabale mwana 
ndipo alibenso Wothandizana naye 
pa Ufumu (Wake). Adalenga 
chinthu chilichonse ndikuchilinga 
Mlingo Wake. 

3. Ndipo m'malo mwa lye 
(Mulungu weniweni, 
Osakhulupirira) adzipangira 
milungu yomwe Siilenga 
chilichonse koma iyo ndiyomwe 
Idalengedwa; ndiponso ilibe 
mphamvu Yodzichotsera masautso 
ngakhale Kudzidzetsera 
zothandiza. Ndiponso Ilibe 
mphamvu zoperekera imfa ndi 
moyo, Ngakhale kuukitsa akufa. 

4. Ndipo osakhulupirira 
akunena: "Ichi sikanthu (Qur'an 
imene Muhammad {SAW}wadza 
Nayo) koma ndi chonama chimene 
Wachipeka, ndipo pachimenechi 
amthandiza Anthu ena (eni 



o^J)f<^j)l^ 


















Surat 25. Al-Furqan Juzu 18 



759 



^A *j*-i 



Y o d\3jti\ 3jj-- 



mabuku)". Kunena zoona, I wo 
(osakhulupirira) adza ndi 
Chinyengo ndi bodza (pazonena 
zawozi). ] 

5. Ndipo (osakhulupirira) 
akunena: "Iyi (Qur'an) Ndi nthano 
za anthu akale zomwe 
(Muhammad {SAW}) 
adazilembetsa. Choncho 
Zikulakatulidwa kwa iye m'mawa 
ndi Madzulo (kuti aloweze)", 

6. Nena: "Adaivumbulutsa 
Yemwe akudziwa Zobisika 
zam'thambo ndi m'hthaka. Ndithu, 
Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, 
(Nchifukwa chake sakukulangani 
mwachangu Pazimene 
mukunenazi)." 

7. Ndipo akunena: "Ndi 
Mtumiki wanji uyu, Womadya 
chakudya Nkumayenda m'misika? 
Kodi b wanji sadatumizidwe 
Mngelo kwa iye kuti azikhala 
Naye limodzi uku akuchenjeza?" 2 












Osakhulupirira amumzinda wa Makka adali kuinyoza Qur'an namati ndi 
Buku labodza limene walipeka yekhayekha Muhammad (SAW) 
ndikumamnamizira Mulungu kuti ndiye walivumbulutsa. Amatinso anthu a 
mabuku ndiwo adamthandiza kulipeka. Zonena zawozi nzabodza zokhazokha 
chifukwa Qur'an yomwe Muhammad akuiwerengayo ili m'charabu osati 
m'chiyuda. 

2 Amamunenera zachipongwe Mtumiki Muhammad (SAW) kuti: "Nchiyani 
watiposa uyu pamene akudzitcha yekha kuti ndi Mtumiki? lye akudya 
chakudya monga momwe ife tidyera, ndipo akuyendayenda m'misika kunka 
nafunafuna zokhalira moyo monga anthu ena onse achitira. Akadakhaladi 
Mtumiki ndiye kuti Mulungu akadampatsa zosowa zake zonse. Ngati alidi 
Mtumiki bwanji Mulungu sadamtsitsire angelo kumwamba kuti azimthandiza? 
Zikadatero apo tikadamkhulupirira." 



Surat 25. Al-Furqan Juzu 18 I 760 I ^ A *j*-» 



V o OlSyiJl 5j^-rf 



8. "Kapena kuponyeredwa 
nkhokwe (Zachuma), kapena 
kukhala ndi Munda ndikumadya 
m'menemo?" Ndipo Osalungama 
akuti: "Ndithudi, Mukutsatira 
munthu wolodzedwa". 

9. Ona momwe akukuponyera 
mafanizo (omwe Sali oyenerana 
nawe, nthawi zina akuti Ndiwe 
wolodzedwa wamisala, wabodza, 
Wophunzitsidwa ndi anthu ena) 
choncho Asokera, ndipo sangathe 
kupeza njira (Yoongoka 
yokunenera) 

10. Watukuka Mwini kupereka 
madalitso Ambiri, Yemwe 
akafuna, akuchitira Zabwino 
kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa 
Tsiku lachimaliziro) Minda 
yamtendere Yomwe pansi pake 
pakuyenda mitsinje; ndipo 
Adzakupangira nyumba 
zikuluzikulu Zachifumu. 

11. Koma akutsutsa zanthawi ya 
Kiyama. Ndipo Tawakonzera moto 
woyaka (iwo) amene Akutsutsa 
zanthawi ya Kiyama 
(Yachimaliziro.) 

12. (Motowo) ukadzawaona 
(naonso nkuuona) Kuchokera 
pamalo apatali, (iwo) adzamva 
Mkwiyo wamotowo ndi mkokomo 
wake. 






ti^tp wj, 6j^^' (j^% 






<Sfoya» 









Surat 25. Al-Furqan Juzu 18 



761 



)A *>» 



Y o Ot$yJ» ijj~> 



13. Ndipo akadzaponyedwa 
m'menemo, pamalo Opanika uku 
manja atanjatidwa Chakukhosi, 
pamenepo adzaitana imfa (Kuti 
iwafike, afe apumule 
Kumasautsowo). 

14. (Tidzawauza): "Lero 
musaitane imfa Imodzi, koma 
itanani imfa zambiri (Ndipo 
simupeza mpumulo koma 
mazunzo okhaokha)". 

15. Nena: (kwa osakhulupirira) 
"Kodi izi ndizo Zabwino, kapena 
munda wamuyaya umene 
Alonjezedwa oopa Mulungu kuti 
udzakhale Mphoto (yabwino) kwa 
iwo ndi kobwerera (Kotamandika)? 

16. "M'menemo adzapeza 
chilichonse chomwe Adzafune. 
Adzakhala m'menemo 
Muyaya.Mtenderewu ndi lonjezo 
lochokera Kwa Mbuye wako pa 
iwo lomwe Adampempha kuti 
adzawakwaniritsire". 

17. Ndipo (kumbuka) tsiku 
limene Adzawasonkhanitse (awa 
osakhulupirira) ndi Omwe adali 
kuwapembedza (monga Yesu, 
Uzairi ndi angelo) kusiya 
Mulungu; adzanena (Mulungu 
kuuza amene ankalambiridwawo): 
"Kodi ndinu mudasokeretsa anthu 
angawa, Kapena ndi okha 
adasokera njira" 









#ltZ\*. "L 












Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 



762 



^ tjA-i 



T O d\3jti\ djj**> 



18. Adzanena: "O, ulemelero 
ukhale kwa Inu! Sizidali zoyenera 
kwa ife kudzikonzera Atetezi 
mmalo mwa Inu, (nanji kuuza 
anthu Kuti azitipembedza). Koma 
mudawasangalatsa Iwo ndi makolo 
awo kufikira adaiwala Malangizo 
(Anu). Ndipo adali anthu 
Oonongeka." 

19. (Mulungu adzati): "Ndithu, 
yakutsutsani (Milungu yanuyo) 
pazimene mwanena (Kuti iwo 
adakusokeretsani). Ndipo simutha 
Kudzichotsera (chilango) ngakhale 
(kupeza) Chithandizo." Ndipo, 
ndithudi, amene achite Zoipa mwa 
inu, tidzamulawitsa chilango 
Chachikulu. 

20. Ndipo palibe pamene 
tidatuma atumiki Patsogolo pako 
koma ndithu iwo, adali kudya 
Chakudya; ankayendanso 
m'misika. Ndipo Tawasankha ena 
mwa inu kuti akhale mayeso Kwa 
ena (popereka masautso kwa 
olungama). Kodi mupirira? Ndipo, 
Mbuye wako ali Wopenya 
(chilichonse). 

21. Ndipo amene alibe 
chiyembekezo Chakukumana nafe 
akunena: "Bwanji angelo 
Satumidwa kwa ife? Kapena 
timuone Mbuye Wathu (kuti 
atitsimikizire kuti ndiwedi 
Mtumiki Wake"? Ndipo Mulungu 



©IjS ^3 



4' 



*\ £» 9 "H\* 9< <\<*\Z *'"9)9\ £*Z 









C \#9 * 






Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 763 H tjA-t YaOiSyliSj^ 



akunena): "Ndithu, adzitukumula 
mmitima mwawo Ndipo anyoza; 
kunyoza kwakukulu." 

22. Tsiku lowaona Angelo, 
sikudzakhala Chisangalalo tsiku 
limenelo kwa Ochimwa, (koma 
lidzakhala tsiku Lochoka moyo 
wawo). Ndipo adzanena (tsiku 
Limenelo): " Ha! Mulungu 
Atitchinjirize" (koma mawu awa, 
Sadzathandiza chilichonse). 

23. Ndipo tidzaidzera ntchito 
Iliyonse (yabwino) imene adachita, 
ndipo Tidzaichita monga fumbi 
louluka (Ponseponse, yopanda 
phindu chifukwa cha 
Kusakhulupirira Mulungu kwawo.) 

24. Anthu akumunda 
wamtendere tsiku limenelo 
Adzakhala ndi mokhala 
mwabwino, ndi Pamalo 
pampumulo wabwino. 

25. Ndipo akumbutse zatsikulo 
pomwe thambo Lidzang'ambika 
ndikudzetsa mitambo ( Yomwe 
idzachititsa chimdima ponseponse) 
Ndipo angelo adzatsika 
ambirimbiri. 

26. Tsiku limenelo ufumu 
wachoonadi ngwa(Mulungu) 
Wachifundo chambiri. Ndipo 
Lidzakhala tsiku lovuta kwa 
osakhulupirira. 


















Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 



764 



M *&\ 



T o OlSyJl 3jj-*» 



27. Ndipo tsiku (limenelo), 
Wosalungama Adzakukuta zala 
zake uku akunena: "Kalanga Ine! 
Ndikadatsata njira ya Mtumiki." 

28. "E, tsoka langa! 
Ndikadapanda kumchita Uje 
kukhala bwenzi wanga 
(nkadapulumuka Lero)" 

29. "Ndithu, adandisokeza 
kufikira ndidasiya Ulaliki (Wa 
Mulungu) utandidzera. Zoonadi, 
Satana amataya munthu (akaona 
kuti Wamgwetsa 

m ' chionongeko) . ' ' 

30. Ndipo Mtumiki (adasuma 
kwa Mbuye wake) Adati: "E, 
Mbuye wanga! Ndithu, anthu 
Anga aisandutsa Qur'aniyi kukhala 
chinthu Chosiidwa, (sakuiwerenga. 
Ndiponso Sakutsata ziphunzitso 
zake)." 

31. Momwemonso Mneneri 
Aliyense tidamkonzera mdani 
wochokera Mwa (anthu) 
oipa.Ndipo Mbuye wako 
Wakwana kukhala muongoli ndi 
Mthandizi (wako). 

32. Ndipo amene 
sadakhulupirire akunena: "Bwanji 
Qur'an yonse siidavumbulutsidwe 
Nthawi imodzi kwa iye? 
Momwemo (Ukuoneramo, 
tikuitumiza Pang'onopang'ono) 
kuti tiulimbikitse mtimaWako ndi 


















Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 765 I > n *>» 



V o OliyaJl 5jj-- 



iyo, ndipo taiyala,Mkayalidwe 
kabwino. 

33. Ndipo sangakubweretsere 
fanizo lililonse Koma 
tikubweretsera choonadi 
(Choyankha fanizolo ndi 
kukudziwitsa) ndi Ku masulira 
kwabwino. 

34. Amene adzasonkhanitsidwe 
Akukokedwa ndi nkhope zawo 
kunka ku Jahanama,iwowo 
Adzakhala pamalo oipa Ndipo 
ngosokera njira (yachoonadi). 

35. Ndipo ndithu, Musa 
Tidampatsa Buku. Ndipo M'bale 
wake Haaruna (Aroni) 
tidamsankha Kukhala nduna (yake). 

36. Ndipo tidati: "Pitani Kwa 
anthu omwe atsutsa Zisonyezo zathu. 
Choncho, Tidawaononga kotheratu." 

37. Naonso anthu a Nuhi, 
Pamene adatsutsa Atumiki, 
Tidawamiza, ndipo tidawachita 
Kukhala phunziro kwa anthu, 
ndipo anthu, Osalungama 
tawakonzera chilango Chowawa; 

38. Nawonso Adi, Asamudu ndi 
eni chitsime Ndi mibadwo 
yambiri Pakati pa iwo. 

39. Ndipo onse tidawaponyera 
mafanizo; ndiponso Onse 
tidawaononga motheratu (pamene 
Adakana kutsatira malamulo athu). 



$taMk&£$S&' 





















©j££ 



Siirat 25. Al-Furqan Juzu 19 I 766 I > 1 *>' t ° atfyil* 5 J>* 



40. Ndipo ndithu, iwo 
(Akuraishi, m'maulendo awo) 
Adafika pamudzi womwe mvula 
yoipa Idawavumbwa. Kodi sadali 
kuuona? Koma sadali 
kuyembekezera Zakuuka ku imfa. 

41. Ndipo akakuona (iwe 
Mtumiki Muhammad {SAW}), 
amangokuchitira chipongwe: 
"Kodi uyu ndi yemwe Mulungu 
wamtuma kuti Akhale mtumiki?" 

42. "Ndithu, adatsala pang'ono 
kutisokeretsa Kumilungu yathu, 
tikadapanda kupirira 
Pamilunguyo" Posachedwapa 
Adziwa, pamene adzaona 
Chilango, (kuti) ndani Wosokera 
zedi njira. 

43. Kodi wamuona yemwe 
wachichita Chilakolako chake 
(chimene akuchikonda) Kukhala 
mulungu wake? Kodi iweyo 
Ungathe kukhala muyang'aniri wa 
iye (Kotero kuti ungamkakamize 
chomwe Safuna)? 

44. Kapena ukuganiza kuti 
ambiri a iwo akumva Kapena 
kuzindikira? Iwo sali kanthu Kena 
koma ali ngati ziweto. Ndipo iwo 
Asokera kwambiri njira. 

45. Kodi sudaone momwe 
Mbuye wako Wautambasulira 
mthunzi? Akadafuna, Akadauchita 
kuti ukhale wokhazikika 



S9'*>'9 / 9 9<9' ' 9S*jrs& \'9' ' 









w**- 






Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 



767 



H *>i 



Y o OtSjiJl 5jj-j 



(Wosasinthasintha). Ndipo 
talichita Dzuwa kukhala 
chisonyezo chake; 1 

46. Kenaka tikuufumbata kwa 
Ife M'kufumbata 
kwapang'onopang'ono (Kufikira 
wonse wutachoka). 

47. Ndipo lye ndi amene 
wakuchitirani usiku Kukhala 
monga chovala, ndipo tulo Monga 
mpumulo, ndipo usana wauchita 
Kukhala monga nthawi youka 
(kuimfa). 

48. lye ndi Yemwe amatumiza 
mphepo Kukhala nkhani yabwino 
Patsogolo pa chifundo Chake 
(mvula), Ndipo kuchokera 
kumitambo Tikutsitsa madzi oyera 

49. Kuti ndi madziwo tiukitse 
dziko lakufa (Lachilala), 
ndikumwetsa Zina mwa zimene 
tidazilenga Monga ziweto ndi 
anthu Ochuluka. 

50. Ndiponso ndithu, tikuigawa 
(mvulayi) pakati Pawo kuti 
akumbukire,ndipo anthu ambiri 
Akukana (kuthokoza Mulungu) 
koma Kupitiriza kusakhulupirira. 



$&>&£ 



e^SS^^S 















1 Apa Mulungu akuti kodi sukuona luso la Mulungu pa zopangapanga Zake 
ndi mphamvu Zake zoposa momwe amautambasulira mthunzi nthawi 
yamasana kuti munthu akhale pamthunzi ndikupeza mpumulo wabwino 
kuchoka mkutentha kwa dzuwa. Pakadapanda mthunzi ndiye kuti munthu 
akadatenthedwa ndi dzuwa ndikusowetsedwa mtendere pamoyo wake. Ndipo 
Mulungu akadafuna akadauleka mthunzi kuti ukhale pamalo amodzi. Koma 
lye ndi mphamvu Zake zoposa adaupanga kukhala wosinthasintha. 



Surat 25. AI-Furqan Juzu 19 768 | ] * *>* 1° Otfjili t^ 



51. Ndipo tikadafuna, 
tikadatuma mchenjezi 
Wawowawo m'mudzi uliwonse, 
(koma Tatuma Muhammad 
{SAW}kutiakhale 
Mchenjezi waonse). 

52. Choncho usawamvere 
osakhulupirira Koma limbana 
nawo ndi iyo (Qur'an); kulimbana 
kwakukulu. 

53. Ndipo lye (Mulungu) ndi 
Yemwe Wazikumanitsa nyanja 
Ziwiri,iyi yamadzi Okoma othetsa 
ludzu Ndi iyi yamadzi amchere 
owawa. Ndipo waika malire ndi 
Chitsekerezo chotsekereza pakati 
pa izo. 

54. Ndipo lye ndiye adalenga 
munthu ndi madzi Ndiponso 
adamchitira chibale cha magazi 
Ndi chibale cha ukwati. Ndipo 
Mbuye Wako ali Wokhoza 
chilichonse. 

55. Ndipo (ena mwa anthu) 
akupembedza Zina zake kusiya 
Mulungu, zomwe 
Sizingawathandize ndiponso 
Sizingawadzetsere masautso 
(atasiya Kuzipembedza). Ndipo 
wosakhulupirira ndi Mthandizi wa 
zoipa poukira Mbuye wake. 

56. Ndipo Ife sitidakutume 
koma kuti ukhale Wouza nkhani 



asftzRStWkss 









*>><*'< 






®©j]^$&$j 



Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 



769 



>^ ^j*-i 



V O d\&jti\ djj-- 



zabwino (okhulupirira); ndi 
Wochenjeza (osakhulupirira). 

57. Nena: "Sindikupemphani 
malipiro Pazimenezi (zomwe 
ndikukuphunzitsani) Koma amene 
afuna ayende panjira Yopita kwa 
Mbuye wake, (Popanda 
chopereka)." 

58. Ndipo tsamira kwa 
(Mulungu) Wamoyo,Wamuyaya 
Yemwe saafa. Ndipo Mulemekeze 
pomtamanda ndi mbiri Zake. 
Ndipo lye akukwana kudziwa 
Bwinobwino machimo a akapolo 
Ake; 

59. Yemwe adalenga thambo 
ndi nthaka ndi Zimene zikupezeka 
mkati mwake. (Adazilenga) 
m'masiku asanu ndi limodzi, 
Ndipo adakhazikika pampando 
Wake Wachifumu (mkukhazikika 
kodziwa yekha). lye 
Ngwachifundo chambiri; 
mufunseni Wodziwa za lye. 

60. Ndipo akauzidwa (kuti): 
"Mulambireni (Mulungu) 
Wachifundo chambiri." Amati: 
"Ndani Wachifundo chambiri? 
Kodi Tilambire Yemwe iwe 
ukutilamula?" (Mawu Amenewa) 
adawaonjezera iwo mwano. 

61. Watukuka Mwini kupereka 
madalitso Yemwe adakhazikitsa 
nyenyezi kuthambo, Ndipo 















j*$& 






Surat 25. AI-Furqan Juzu 19 770 \ * *j*-» Y otSytfi oj^» 



m'menemo adaika nyali (dzuwa) 
Ndi mwezi wounika; 

62. Ndipo lye ndi Yemwe 
adapanga usiku Ndi usana kuti 
zizitsatana (Ndikusinthana). (Izi 
zingapindulitse) kwa Amene afuna 
kukumbukira kapena (amene) 
Afuna kuthokoza. 

63. Ndipo akapolo a (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri ndi omwe 
akuyenda padziko Modzichepetsa, 
ndipo Mbuli zikanena kwa iwo 
(Mawu amwano), amaziyankha 
Mawu abwino. 

64. Ndi omwe amapititsa 
nthawi inaYausiku uku akulambira 
ndi kuimirira Chifukwa 
chakulemekeza Mbuye wawo; 

65. Ndi omwe akunena, "E, 
Mbuye Wathu tichotsereni 
Chilango cha Jahannama; Ndithu, 
chilango chake Nchosasiyana 
nacho. 

66. "Ndithu, iyo ndi malo 
woipa; Ndiponso pokhala poipa." 

67. Ndi omwe amati 
akamagawira anthu ena Chuma 
chawo, samwaza pachabe 
ndiponso Sachita umbombo, koma 
amachita Mwapakatikati. 

68. Ndi omwe sapembedza 
milungu ina Poiphatikiza ndi 
Mulungu, ndiponso Saapha 









^%lli|ij(^i &&£&i$3 






^fffeJSW^""'^ 









Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 



771 



H *>i 



To d\3jal\ Ojj-*> 



munthu yemwe Mulungu adaletsa 
Kumupha kupatula pakakhala 
choonadi Ndiponso saachita 
chigololo. Ndipo amene achite 
zimenezi, apeza Masautso 
(pompano padziko lapansi). 

69. Chilango 
chidzawonjezeredwa kwa iye 
Tsiku la Kiyama, ndipo adzakhala 
M'chilango muyaya uku ali 
wonyozeka; 

70. Kupatula amene walapa, 
Naakhulupirira, ndikuchita ntchito 
Yabwino. Tsono iwowo, Mulungu 
Adzawasinthira zoipa zawo 
kukhala Zabwino. Ndipo Mulungu 
ali Wokhululuka Kwambiri, 
Wachisoni, 

71. Ndipo amene akulapa 
ndikuchita zabwino, Ndithu, iye 
akulapa mwachoonadi kwa 
Mulungu. 

72. Omwenso sachitira umboni 
zabodza, Ndipo akadutsa pamalo 
pazachibwana, Amadutsa 
mwaulemu; 

73. Ndiponso omwe amati 
akakumbutsidwa Aya za Mbuye 
wawo, samazigwera Mwaugonthi 
ndi mwakhungu; 

74. Ndi omwenso akunena: "E, 
Mbuye wathu Tipatseni mwa akazi 
athu ndi ana Athu chotonthoza 



Qys%&&Jz%&h 



&' 












is* 



^VJ&Pi 






Surat 25. Al-Furqan Juzu 19 I 772 I \ * fjA-i Y d&jd\ oj^ 



maso, ndipo tichiteni Kukhala 
atsogoleri A oopa Mulungu." 

75. Iwo adzalipidwa nyota 
Zapamwamba chifukwa Cha 
mavuto omwe Adawapirira. Ndipo 
Akalandira m'menemo Ulemu ndi 
mtendere, 

76. Akakhala m'menemo 
muyaya; malo abwino Ndi 
pokhala pabwino. 

77. Nena, "Ndithu,Mbuye 
wanga sakadalabadira Chilichonse 
pa inu pakadapanda Mapemphero 
anu, (akadakulangani pompano 
Padziko lapansi.) Komabe inu 
mwatsutsa (Uthenga wa aneneri). 
Choncho chilango 
Chidzakugweranibe." 






@M2Uj\ ffi »*«£*..rS^^fl^> 







Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



773 



H *>» 



V 1 *ly*JiJl Ojj--. 




M'surayi muli izi:- Kumayambiriro kwake yafotokoza 
zaulemelero wa Qur'an. Ndiponso yaopseza okanira onse kuti 
Mulungu akhoza kuwatsitsira chilango pompano padziko 
lapansi. Ndipo yamtonthoza Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye) pamasautso amene adakumana nawo kwa anthu 
ake pomufotokozera zamasautso omwe atumiki anzake 
adakumana nawonso kuchokera kwa anthu awo. Yafotokozanso 
zakukumana kwa Musa, Haarruna ndi Farawo, ndikuti Farawo 
adatsutsa uthenga wa awiriwa. Ndipo yafotokozanso nkhani ya 
Ibrahim yemwe ndikholo la aneneri, ndi nkhani ya Nuhi 
pamodzi ndi anthu ake; ndi nkhaninso ya Hudu pamodzi ndi 
Adi, ndi nkhaninso ya Swaleh pamodzi ndi Asamudu. 

Ndipo surayi yafotokoza mwatsatanetsatane za ulaliki wa 
Luti ndi Shuaibu. Ndipo wolingalira aona m'nkhani za anenerizi 
kuti maziko a ulaliki wawo ndi amodzi; ndikuti njira ya otsutsa 
ndi imodzinso poukana uthenga wa aneneri wo. 

Surayi yamaliza ndikunena za ulemerero wa Qur'an monga 
momwe yafotokozera kumayambiriro kwake. Ndipo yanena, 
komalizirako, kuti Qur'an sindakatulo. 




Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 I 774 I \ * *> 



T *\ *1yuiJl 3jj-*> 



Surat Ash-Shu'ara XXVI 






M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Td-Sin-Mtm. 

2. Izi ndi aya za Buku (la 
Qur'an) lofotokoza Chilichonse 
(chofunika m'chipembedzo). 

3. Mwina iwe (Mtumiki 
Muhammad{SAW}) Udziononga 
wekha (ndi madandaulo) 
Chifukwa chakuti (iwo) sadakhale 
Asilamu. 

4. Tikadafuna, tikadawatsitsira 
chizizwa Kuchokera kumwamba; 
makosi awo Akadadzichepetsa ndi 
chizizwacho,(sakadatha 

Kucheukira kwina koma sitifuna 
kukakamiza Anthu kuti akhale 
Asilamu). 1 

5. Ndipo palibe pamene 
chikuwadzera Chivumbulutso 
chatsopano chochokera kwa 
(Mulungu) Wachifundo chambiri 
koma Amazipatula ku icho 
(chivumbulutso). 



wm&'hm 



oA^t^jlt^l, 



©. 






»j 






1 Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adali 
kuwawidwa mtima kwambiri poona kuti anthu sakuvomereza uthenga 
wachoonadi umene iye adadza nawo, ndipo adali kuwamvera chisoni 
kwambiri. Choncho Mulungu adamtonthoza pomuuza kuti "Usadziphe wekha 
chifukwa chokhala ndi maganizo owamvera chisoni". Mulungu akadafuna 
kuwaongola mowakakamiza akadatha kutero; koma sadafune. 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



775 



^ fr>1 t *\ t\jLXS\ OjJ- 



6. Ndithu, atsutsa; choncho 
posachedwapa Ziwadzera nkhani 
zomwe adali kuzichitira 
Chipongwe. 

7. Kodi sadaone nthaka? Ndi 
mmera ungatiTaumeretsa 
m'menemo wamtundumtundu, 
Wokongola? 

8. Ndithu, m'zimenezo muli 
zizindikiro (Zosonyeza mphamvu 
za Mulungu). Koma Ambiri a iwo 
sali okhulupirira. 

9. Ndipo, ndithu, Mbuye wako 
ndi mwini Mphamvu zoposa; 
Wachisoni. 

10. Ndipo (akumbutse) Pamene 
Mbuye wako adaitana (m'neneri) 
Musa; adamuuza:"Pita kwa anthu 
ochita zoipa, 

11. Anthu a Farawo; (auze): 
Kodi sawopa (Mulungu)?" 

12. (Musa) adati: "Mbuye 
wanga! Ine ndikuopa Kuti 
anganditsutse; 

13. Ndipo chingabanike 
chifuwa changa (ndi Maganizo, 
chifukwa chakunditsutsa kwawo); 
Ndiponso lirime langa siliyankhula 
Momveka bwino. Choncho 
tumizaninso Uthengawu kwa 
Haaruna (kuti tikhale awiri Ndipo 
azikandithangata pantchito 
yangayi). 






^%e^jSi«K^ 






^&&s&m& 



CHJ&&* 



ty*38$&a$>& 









Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



776 



\ * frjJrl Y ^ *\jl*}\ djj^ 



14. Ndipo iwowo ndili nawo 
mlandu Ndipo ndikuopa kuti 
angandiphe (Pobwezera chimene 
ndidawalakwira Powaphera 
munthu wawo). 

15. (Mulungu) adati: Iyayi! 
Pitani Pamodzi ndi zozizwa Zathu; 
ndithu, Ife Tikakhala nanu limodzi 
(pokuthangatani) Uku 
tikumvetsera (zimene azikanena). 

16. Choncho mpitireni Farawo, 
ndipo Kamuuzeni kuti: "Ife ndi 
atumiki Ambuye wa zolengedwa 
zonse;" 

17. (Tatumidwa) kuti 
uwapereke kwa ife Ana a Isiraeli 
(kuti tinke nawo ku Shamu)." 

18. (Farawo) adati (kwa Musa): 
"Kodi Sitidakulere kwathu uli 
mwana, ndi kukhala Nafe pamoyo 
wako zaka zambiri? 

19. Ndipo udachita chochita 
chako chimene Udachichita, ndipo 
iwe ndiwe mmodzi wa Osathokoza!" 

20. (Musa) adati: "Ndidachita 
zimenezo Pomwe ine ndidali 
mmodzi wa osazindikira Zinthu. 

21. Choncho ndidakuthawani 
pomwe Ndidakuopani; tsono 
Mbuye wanga Wandipatsa nzeru 
zoweruzira (zinthu), ndi 
Kundisankha kukhala mmodzi wa 
atumiki. 



1 $$%3&&2&ffi& 






^zm$&M 



ftSBgs^aa 



mj^j^^^m^ 



W5 



y S9 '\ 9 9 



&^£&$@S*££& 






Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



777 1 ^ *j*-l T 1 ttyutJl 3jj-- 



22. Ndipo kodi umenewu 
ndimtendere Wonditonzera pomwe 
mudawaika muukapolo Ana a 
Israeli!" 

23. Farawo adati: "Kodi ndani 
Mbuye Wazolengedwayo?" 

24. (Musa) adati: "Mbuye wa 
thambo ndi nthaka Ndi zapakati 
pake, ngati muli ndi 
Chitsimikizo . ( Amachita 
chilichonse M'menemo mmene 
wafunira; kupereka Moyo ndi 
imfa)." 

25. (Farawo) adauza omwe 
adali m'mphepete Mwake 
(mwachipongwe): "Kodi 
simukumva (Mawu 
achibwanawa)?" 

26. (Musa adapitiriza kunena) 
adati: "Mulungu Ndi Mbuye Wanu 
komanso Mbuye wamakolo Anu 
oyamba". 

27. (Farawo) adati (kwa anthu 
ake pofuna Kuwakwiitsa): 
"Ndithu, Mtumiki Wanu amene 
watumidwa kwa inu, Ngwamisala". 

28. (Musa) adati "Mbuye 
wakuvuma ndi Kuzambwe, ndi 
zomwe ziri pakati pake Ngati 
mumazindikira (zinthu, 
Muzindikira izi)". 

29. (Farawo) adati: "Ngati 
udzipangira mulungu Wina kusiya 



8&^5^ftM& 






%^m^^^ 



®ri&&>\ 



vtm\>x$&z%yjs 






98®&$W&&t$$S 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



778 H *j*-» 



Y *\ *tyuiJl 3jj-- 



ine, ndikuchita Kukhala mmodzi 
wa omangidwa kundende." 

30. (Musa) adati: "Kodi 
ngakhale Nditakubweretsera 
chinthu choonekera Poyera 
(chosonyeza kuti zimene 
ndikunenazi Ndizoona 
ndatumidwa ndi Mulungu)? 

31. (Farawo) adati 
"Chibweretse, ngati uli Mwa 
onena zoona." 

32. Ndipo (Musa) adaponya 
(pansi) ndodo Yake, mwadzidzidzi 
idasanduka njoka Yopenyeka. 

33. Ndipo adautulutsa mkono 
wake; pompo Udali woyera 
(kwambiri) kwa (onse) Openya. 

34. (Farawo) adauza akuluakulu 
omwe adali M'mphepete mwake: 
"Ndithu, uyu ndi Wamatsenga 
wodziwa kwambiri; 

35. Akufuna kukutulutsani 
m'dziko lanu ndi Matsenga ake; 
kodi Nanga mukuti chiyani?" 1 

36. (Anthu) adati (kwa Farawo): 
"Mpatse nthawi Ndi mbale 
wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) 
M'mizinda yonse osonkhanitsa 
anthu. 









1 Farawo adasimidwa, adatha nzeru zedi ndi mawu amene adali kutuluka 
m'kamwa mwa Musa kotero kuti adangoti kakasi, kusowa chonena, nayamba 
kuwafunsa nzeru ndi malangizo anthu ake pomwe iye ankadzitcha kuti 
ndimulungu wodziwa zonse, wamphamvu zoposa. 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



779 



y ^ frj^ri r n t iy^J» o^^ 



37. Ndipo akubweretsera 
amatsenga onse Odziwa kwabasi 
(kotero kuti adzampambana 
Musa)" 

38. Choncho amatsenga 
adasonkhanitsidwa M'nthawi ya 
tsiku lodziwika, 

39. Ndipo anthu adaudzidwa: 
"Kodi inu Musonkhana? (choncho, 
sonkhanani). 

40. Mwina tingawatsatire 
Amatsenga ngati iwo Ndiamene 
apambane." 

41. Ndipo pamene amatsenga 
Adadza,adati kwa Farawo: "Kodi 
tidzakhala ndi mphoto Ngati ife 
ndife tipambane?" 

42. (Farawo) adati: "Inde, 
(ndipo kuonjezera apo) Ndithu inu 
mudzakhala mwa amene 
Amakhala pafupi (ndi ine, monga 
nduna Zanga)". 

43. Musa adati kwa iwo: 
"Ponyani zimene Mufuna kuponya 
(zosonyeza kuya kwa Matsenga 
ami)." 

44. Choncho adaponya zingwe 
zawo ndi ndodo Zawo, ndipo adati: 
"Kupyolera m'mphamvu Za 
Farawo, ndithu, ife ndife opambana." 

45. Kenako Musa adaponya 
yake; Mwadzidzidzi iyo idameza 
zabodza Zomwe iwo adakonza. 



®*W*:#3$r 



k$2&&$?&r& 



*%^%&M£& 









etgB&foSStif&XCfi 






as&W 



Sfirat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



780 



1 ^ *j*-» Y *\ tljuJJl 0^^ 



46. Pamenepo amatsenga 
adazigwetsa pansi Molambira, 

47. Adati: "Tamkhulupirira 
Mbuye Wazolengedwa, 

48. Mbuye wa Musa ndi 
Haaruna." 

49. (Farawo) adati: "Ha! 
Mwamkhulupirira Chotani 
ndisanakulolezeni? Ndithu, Iyeyu 
ndimkulu wanu amene 
Adakuphunzitsani matsenga. 
Choncho Posachedwa mudziwa 
(Chimene ndikuchiteni)ndithu 
ndidula manja anu ndi miyendo 
yanu Mosinthanitsa (podula 
mkono wakumanja Ndi mwendo 
wakumanzere; kapena Kudula 
mkono wakumanzere ndi mwendo 
Wakumanja), ndipo kenako 
Ndikupachikani nonsenu." 

50. (Amatsenga) adati: "Palibe 
vuto, ndithu, Ife (tonse) tibwerera 
Kwa Mbuye wathu" 

51. Ndithu, ife tikuyembekezera 
kuti Mbuye wathu atikhululukire 
zolakwa Zathu; pokhala oyamba 
Mwa okhulupirira". 

52. Ndipo tidamvumbulutsira 
Musa (kuti): "Pita ndi anthu anga 
m'nthawi yausiku (Musamuke 
m'dziko la Iguputo); ndithu, Inu 
mutsatidwa." 

53. Choncho Farawo adatuma 
(owatuma) Kuti asonkhanitse 












«Qs» 






&t'*£L.&C&\?.Z:; 



V&9-y#0^\&{&tti 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



781 



> H frj^rl 1 1 frlycJJt 5jj-- 



anthu m'mizinda (Kuti aletse 
Ayuda kutuluka). 

54. (Adawauza otumidwa aja 
kuti auze Anthu kuti): "Ndithu, 
awa (Ayuda) Ndikagulu kochepa, 

55. Ndipo iwo akutikwiitsa; 

56. Koma ife tonse(ndife 
ochuluka komabe Ngakhale zili 
choncho) tikuwaopa." 

57. Choncho tidawatulutsa 
m'minda ndi Mwa akasupe, 

58. Ndi m'nkhokwe zachuma 
ndi m'malo Okongola; 

59. Momwemo ndi mmene 
tidawachitira Ndipo 
tidawalowetsera chokolo Zinthu 
zawo zonse kwa ana a Israeli. 

60. Choncho (anthu a Farawo 
ndi iye mwini) Adawatsatira 
(Ayuda) dzuwa Litatuluka. 

61. Ndipo pamene magulu awiri 
adaonana (Anthu a Farawo ndi 
Ayuda), anthu a Musa adati: 
"Ndithu, ife Tigwidwa." 

62. (Musa) adati: "Iyayi! Ndithu 
Mbuye wanga ali nane 
pamodzi.Andiongolera (kuti ife 
tonse Tipulumuke)." 

63. Ndipo tidam'vumbulutsira 
mawu Musa (Akuti):"Menya 
nyanja ndi ndodo Yako." Ndipo 



%$£*$&& 



^'^fatf!'* 






<fe 9P<* \ ' 9 * 9*\9*9$f 






/^iSu^I^^\(j^(J3tj*-jSa 



Surat 26. Ash-Shu ara Juzu 19 



782 



>* tjk-\ y i t\jL±)\ oj^ 



idagawikana, mbali Iliyonse idali 
ngati phiri lalikulu. 

64. Ndipo tidawayandikitsa 
pamenepo Anthu enawo, (Farawo 
ndi anthu ake Nalowa panjira 
yomweyo pambuyo pa Musa Ndi 
anthu ake). 

65. Ndipo tidapulumutsa Musa 
ndi onse Amene adali nawo 
(mpaka adaolokaNyanjayo, madzi 
ali chiimire Mbali iyi ndi iyi). 

66. Kenako tidawamiza enawo, 
(Farawo Ndi anthu ake). 

67. Ndithu, pazimenezi pali 
lingaliro. Koma ambiri aiwo sali 
okhulupirira. 

68. Ndipo, ndithu Mbuye wako 
ndimwini Mphamvu zoposa 
(amalanga ndi Chilango choopsa 
omwe amunyoza); Wachisoni 
(kwa omkhulupirira Ndi 
kumumvera). 

69. Ndipo awerengere 
(osakhulupirira) Nkhani ya 
(M'neneri) Ibrahim, 

70. Pamene adafunsa bambo 
wake ndi anthu Ake (kuti): "Kodi 
mukupembedza Chiyani?" 

71. Adati: "Tikupembedza 
mafano; Ndipo tipitiriza 
kuwapembedza." 

72. (Ibrahim) adati: "Kodi 
amakumvani Mukawaitana 









®t*ms%i 









Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 I 783 I > * *j*-» t n ^iyuiJi Sj^ 



73. kapena amakuthandizani 
(Mukawapembedza) kapena 
amapereka Masautso kwa inu 
(mukasiya kuwapembedza)? 

74. (Iwo) adati: "Koma tidapeza 
makolo athu Akuchita zimenezi." 

75. (Ibrahim) adati: "Kodi 
mukuona awa Amene mwakhala 
mukuwapembedza, 

76. Inu ndi makolo anu amene 
adatsogola? 

77. Ndithu, iwo ndiadani anga, 
Kupatula Mbuye wa zolengedwa 
zonse; 

78. Yemwe adandilenga, 
ndiponso Yemwe Akundiongolera 
(kunjira yolungama); 

79. Ndiyemwe akundidyetsa ndi 
Kundimwetsa. 

80. Ndipo ndikadwala 
ndiyemwe Amandichiritsa. 

81. Ndi Amene adzandipatsa 
imfa, ndipo (Tsiku la Kiyama) 
adzandidzutsa; 

82. Ndi Yemwe 
ndikuyembekezera kuti 
Adzandikhululukira zolakwa zanga 
Tsiku la malipiro. 

83. E, Mbuye wanga! 
Ndipatseni nzeru Zoweruzira 
(zinthu), ndikundilumikiza Ndi 
anthu abwino; 






%SXZ 



^mo0^'^^ 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



784 



> * ftjA-» x l t\jcxl\ ojf 



84. Ndipatseni kutchulidwa 
Kwabwino kwa anthu ena Odza 
pambuyo; 

85. Ndichiteni kukhala mmodzi 
Mwa olandira munda wamtendere; 

86. Ndipo khulukirani bambo 
wanga; Ndithu, iye adali mmodzi 
wa osokera; 

87. Ndipo musadzandiyalutse 
patsiku Loukitsidwa anthu (ku 
imfa); 

88. Tsiku lomwe chuma ndi ana 
Sizidzathandiza (aliyense) 

89. Kupatula yemwe adzadza 
kwa Mulungu Ndi mtima woyera 
(iye ndiamene Adzathandizidwa 
patsikulo);" 

90. Ndipo munda wamtendere 
Udzayandikitsidwa kwa oopa 
(Mulungu), 

91. Ndipo Jahannama 
idzaonetsedwa kwa opotoka; 

92. Ndipo kudzanenedwa kwa 
iwo: "Ali kuti amene mudali 
kuwapembedza aja, 

93. M'malo mwa Mulungu? 
Kodi angathe Kukuthandizani 
kapena Kudzithandiza okha?" 

94. Ndipo iwo ndi opotoka ena 
adzaponyedwa Ndi nkhope zawo 
M'menemo (mu Jahannama). 



"^.t 



' 9<j^Au,5*?"^ 



^wwass&a&i; 



Gi&^&j^ 



W"XX ^Ul,'^ '&!&i / *\l': 1 1 






**Wff$$. 



®j&<J&M&% 



®0^&\<Ml 



®, 



%$&%<&. 



*% 



® (^liJ^S^l^W'^^ls 



X< *>>>.' Y± i\ >* » 






%&\#^& 



Siirat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 785 ^ * *j*-i X 1 ^y^\ oj^ 



95. Ndi magulu onse ankhondo 
a Iblis (Omwe adali kukometsa 
kwa anthu Zoipa ndi machimo). 

96. Adzanena (movomereza 
kulakwa kwawo) Uku naonso ali 
m'menemo, akukangana (Ndi 
anzawo omwe adawasokeretsa): 

97. "Ndikulumbira Mulungu, 
ndithu, Tidali m'kusokera 
kowonekera. 

98. Pamene timakufananitsani 
Ndi Mbuye wazolengedwa. 

99. Ndipo sadatisokeretse 
(onse) Koma oipa okha basi. 

100. Choncho ife tilibe aomboli 
(Otiombola), 

101. Ngakhalenso bwenzi 
wapamtima (Woti angatipulumutse 
kumasautsowa). 

102. Tikadapeza mwayi 
wobwerera (kumoyo Wapadziko), 
tikadakhala Mwa okhulupirira." 

103. Ndithu, m'zimenezi, muli 
malingaliro Aakulu, koma ambiri 
Aiwo sali okhulupirira. 

104. Ndipo ndithu, mbuye 
wako, ndiye Mwini mphamvu 
zoposa; Wachisoni. 

105. Anthu a Nuhi adatsutsa 
atumiki. 

106. Pamene adawauza Nuhi 
m'bale Wawo kuti: "Kodi 






<£y »-? <sr \"j jgiffi 






v 



®'i.-X>Arr~ 



®k 



*&£<&& 



®&^z&m®& 






%mj>£*%& 



<$3G$&&&m 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



786 



\ * *j*-» V \ i\jK±S\ 5jj-- 



simufuna kuopa (Mulungu 
ngakhale nditakuuzani zoopsa 
Zimene zikukudikirani)? 

107. Ndithu, ine kwa inu ndine 
Mtumiki Wokhulupirika; 

108. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni. 

109. Ndipo sindikupemphani 
malipiro pazimenezi; Malipiro 
anga ali kwa (Mulungu) Mbuye 
wazolengedwa. 

110. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni." 

111. (I wo) adati: "Nchotani kuti 
tikukhulupirire Iwe chikhalirecho 
anthu wamba ndi Amene 
akukutsatira?" 

112. (Nuhi) adati: 
"Sindikudziwa zimene Adali 
kuchita (zomwe zachititsa kuti 
Mulungu awaongolere kunjira 
yoongoka). 

113. Chiwerengero chawo 
sichili kwina Koma kwa Mbuye 
wanga, mukadakhala 
Mukuzindikira. 

114. Ndipo sindine wopirikitsa 
okhulupirira (Ku chipembedzo cha 
Mulungu kuti Inu olemekezeka 
muchikhulupirire) . 

115. Ine sikanthu , koma ndine 
mchenjezi Woonekera." 






M^mz&&]&&.j 



vj 






s^$&&ffc*a 



'* ^«5i r^r-^P^ 



yjh$»\0 



©^&s*6f<a 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



787 



M *>l V\ tljiuSJl 3jj~> 



116. (Iwo) adati: "Ngati susiya, 
iwe Nuhi, Zonena zakozi) ukhala 
mmodzi mwa Ogendedwa (miyala 
mpaka ufe)." 

117. (Nuhi) adati (kwa 
Mulungu): "Mbuye Wanga! 
Ndithu anthu anga anditsutsa. 

118. Choncho weruzani pakati 
panga ndi Pakati pa iwo 
(chiweruzo chabwino), Ndipo 
ndipulumutseni pamodzi ndi 
amene Alinane mwa okhulupirira." 

119. Choncho, tidampulumutsa 
pamodzi ndi Omwe adali naye 
m'chombo chodzadza (Ndi 
chilichonse chamoyo chomwe 
Chidalipo m'dziko, chachimuna 
ndi Chachikazi chidaikidwa 
m'menemo). 

120. Pambuyo pake tidawamiza 
otsalawo. 

121. Ndithu, m'zimenezi muli 
malingaliro; Koma ambiri a iwo 
Sadali okhulupirira. 

122. Ndipo ndithu, Mbuye 
wako, lye Ngwamphamvu zoposa; 
Ngwachisoni 

123. Naonso Adi adatsutsa 
atumiki. 

124. Pamene m'bale wawo 
(Mneneri) Hud Adawafunsa kuti; 
"Kodi simuopa Mulungu? 






#^«#<&#ae 



" £ 9 " 9 *<£&*< 9 )*9" 9 9S9+KK* 






©(• ** '- 



k^^&^s&^SR 












Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



788 



\ * ftj*-* r ^ tiyuJi d J>( - 



125. Ndithu, ine ndine Mtumiki 
wokhulupirika Kwa inu; 

126. Choncho, muopeni 
Mulungu ndipo Mverani ine. 

127. Ndipo pazimenezi 
sindikukupemphani Malipiro; 
ndithu, malipiro anga ali Kwa 
(Mulungu) Mbuye wazolengedwa. 

128. Kodi mukudzimangira 
nyumba pamalo Paliponse 
pachitunda, pokongola 
Moseweretsa? 

129. Ndipo mukudzimangira 
(nyumba zonga) Linga ngati kuti 
mukuona kuti Mudzakhala muyaya? 

130. Ndipo mukamamenya 
Nkhondo mumamenya 
Modzitukumula. 

131. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni. 

132. Ndipo muopeni Yemwe 
adakupatsani Zimene mukuzidziwa. 

133. Adakupatsani ziweto ndi ana, 

134. Ndi minda ndi akasupe. 

135. Ndithu, ine 
ndikukuoperani chilango Cha tsiku 
lalikulu." 

136.Adati:"Kwaife 
nchimodzimodzi, Utichenjeze 
kapena iwe usakhale Mmodzi mwa 
ochenjeza. 









i >&A"i/. v:f?\*\"\§ 



&&&\<&$%2 



Siirat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



789 



> ^ *>i r n i\j*^\ ojj-* 



137. Ndithu, kutero (anthu ena 
Kudzitcha atumiki a Mulungu), 
sikanthu Koma ndi machitidwe a 
anthu akale. 

138. Ndipo ife sitidzalangidwa 
(monga Mom we ukunenera)." 

139. Choncho adamtsutsa, 
ndipo Tidawaononga. Ndithu, 
m'zimenezi muli Malingaliro; 
koma ambiri aiwo sadali 
Okhulupirira. 

140. Ndipo ndithu, mbuye wako 
ndiye Wamphamvu zoposa; 
Wachisoni. 

141. A Samudu (naonso) 
adatsutsa atumiki. 

142. Pamene m'bale wawo 
Swaleh Adawauza kuti: "Kodi 
simuopa (Mulungu) 

143. Ndithu, ine ndimtumiki 
wokhulupirika Kwa inu. 

144. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Mverani ine. 

145. Ndipo sindikupemphani 
malipiro Pazimenezi. Palibe 
kumene kuli Malipiro anga koma 
kwa Mbuye Wazolengedwa. 

146. Kodi (mukuganizira kuti) 
mudzasiidwa Mwamtendere pa izi 
zili pano (Popanda imfa 
kukudzerani?) 

147. M'minda ndi muakasupe, 



-■mim&a 






®*£$£&4$&j 



^\''>\>'>\,''?<( 






a.^ w\>''*h't 



^ssw 



W^&4$2fc 



'»<\\\>» ' 



*.-> V 



S&JfyE&SBS 






Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



790 



> ^ «.j*-i r n *\jl^\ «j>-» 



148. Ndi (m'minda) yammera 
ndi mitengo Yakanjedza yamikoko 
yakupsa yofewa? 

149. Ndipo mukujoba nyumba 
m'mapiri Mwaluso. 

150. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni. 

151. Ndipo musamvere za awo 
opyola malire, 

152. Amene akuononga 
padziko, ndipo Sakonza." 

153. (Iwo) adati: "Ndithu, iwe 
ndi mmodzi Wa olodzedwa. 

154. Iwe suli kanthu, koma 
munthu ngati ife; Tabwera ndi 
chozizwitsa, ngati Ndiwedi 
mmodzi wa onena zoona!" 

155. (lye) adati: 
"(Ndakubweretserani) Ngamira iyi 
yaikazi; (koma) ikhale Ndi gawo 
lake lakumwa, ndipo inu 
Mukhalenso ndi gawo lanu 
lakutunga (Madzi) patsiku 
lodziwika. (Tsiku Lina lotunga 
madzi anthu). 

156. Ndipo musaikhudze ndi 
choipa chilichonse Kuopera kuti 
chingakupezeni chilango cha Tsiku 
lalikulu." 

157. Koma iwo adaipha; ndipo 
adali odandaula (Pamene chidadza 
Chilango cha Mulungu). 






*e&i$3Bsa; 












Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



791 



M *>l Yn ^lyt^JlSjj-- 



158. Choncho chilango cha 
Mulungu Chidawaononga ndithu, 
pazimenezi pali Phunziro; koma 
ambiri aiwo sadali Okhulupirira. 

159. Ndipo, ndithu, Mbuye 
wako, lye Ngwamphamvu zoposa; 
Wachisoni 

160. Anthu a Luti adatsutsa 
atumiki. 

161. Pamene m'bale wawo Luti 
Adanena kwa iwo (kuti): "Kodi 
Simuopa (Mulungu)? 

162. Ndithu, ine ndine Mtumiki 
Wokhulupirika kwa inu. 

163. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni 

164. Ndipo sindikupemphani 
malipiro Pazimenezi; palibe 
komwe kuli malipiro Anga koma 
kwa Mbuye wazolengedwa. 

165. Kodi mukugonana ndi 
amuna (anzanu) Muzolengedwa 
(za Mulungu), 

166. Ndikusiya amene Mbuye 
wanu Adakulengerani kuti akhale 
akazi anu? Ndithu, inu ndinu anthu 
Olumpha malire." 

167. (Iwo) adati: "Ngati susiya 
(izi), E, iwe Luti! ndithu, ukhala 
mmodzi Wa opirikitsidwa." 

168. (lye) adati: "Ndithu, ine 
ndine m'modzi Wakuzida izi 



A'tfiu* 









Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



792 



>* ftjJt-i Yn tiyuiJidj^- 



zochita zanu (choncho Sindisiya 
kuzidzudzula). 

169. E, Mbuye wanga! 
Ndipulumutseni ine Ndi banja 
langa ku (matsoka a) zimene 
Akuchita.!" 

170. Ndipo tidampulumutsa iye 
ndi onse a pa Banja lake, 

171. Kupatula nkhalamba 
yaikazi (imene Idasankha kukhala) 
mwaotsalira pambuyo. 

172. Titatero tidawaononga 
enawo. 

173. Ndipo tidawavumbwitsira 
mvula (yamiyala); Iyipirenji, 
mvula Ya ochenjezedwa! 

174. Ndithu, pazimenezi pali 
malingaliro. Koma ambiri a iwo 
Sadali okhulupirira. 

175. Ndipo, ndithu, Mbuye 
wako, Ngwamphamvu Kwambiri; 
Ngwachisoni. 

176. Anthu a m'dziko 
lamitengo yambiri (Madiana) 
adatsutsa atumiki. 

177. (Akumbutse) pamene 
(Mneneri) Shuaibu adati kwa iwo: 
"Kodi Simuopa (Mulungu)? 

178. Ndithu, ine ndine Mtumiki 
Wokhulupirika kwa inu. 

179. Choncho muopeni 
Mulungu ndipo Ndimvereni 



%&&asof$ 









Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



793 > * *ji-i t *\ tiytJJi djj-- 



180. Ndipo sindikupemphani 
malipiro Pazimenezi; kulibe 
malipiro anga Koma kwa 
(Mulungu) Mbuye wa zolengedwa. 

181. Kwaniritsani mulingo 
(pamalonda pamene Mukupima), 
ndipo musakhale mwaopungula 
(Mulingo). 

182. Ndipo yesani ndi sikelo 
yolungama (Yolondola). 

183. Ndipo musawachepetsere 
anthu zinthu Zawo, ndiponso 
musayende padziko uku 
Mukuononga. 

184. Ndipo muopeni amene 
adalenga inu Ndiponso 
zolengedwa zoyamba (zimene 
Zidanka kale)" 

185. (Iwo) adati: "Ndithu, iwe 
ndi mmodzi Wa olodzedwa. 

186. Ndipo iwe suli kanthu 
koma munthu ngati Ife, ndipo 
ndithu, tikukutsimikizira Kuti 
ndiwe mmodzi wa abodza. 

187. Choncho tigwetsere 
zidutswa za thambo (Kuti 
zitiononge) ngati uli mmodzi Wa 
onena zoona." 

188. (Shuaibu) adati: "Mbuye 
wanga Ngodziwa kwambiri 
zimene mukuchita. (Akadzaona 
kuti inu ngoyenera Kulangidwa 



m<sjZv$&&$&ts 



®^\g> 



&(*^&1&%3^%\ 









K hr 



&2t > 4 



<y$ 



<&&&$&$ 



Siirat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 794 ^ S *jfci y n f.\yjJ\ Sj^ 



ndizidutswa za thambo, 
Adzakulangani). 

189. Koma adamutsutsa. Ndipo 
chidawagwera Chilango chatsiku 
la mthunzi; ndithu, Chimenecho 
chidali chilango cha Tsiku lalikulu. 

190. Ndithu, pazimenezi pali 
lingaliro; Koma ambiri a iwo 
sadali okhulupirira. 

191. Ndipo, ndithu, Mbuye 
wako Ngwamphamvu kwambiri; 
Ngwachisoni. 

192. Ndipo, ndithu iyi (Qur'an) 
ndiyo chivumbulutso Cha Mbuye 
wazolengedwa zonse. 

193. Mzimu Wokhulupirika 
(Jiburil) Udaivumbulutsa. 

194. Pamtima wako kuti ukhale 
mmodzi wa Achenjezi, 

195. M'chilankhulo cha 
Chiarabu chomveka Bwino. 

196. Ndipo ndithu, izi (zomwe 
zili m'Qur'an) Zilipo m'mabuku 
akale. 

197. Kodi sipadapezeke 
chisonyezo kwa iwo Kuti 
akuidziwa (Qur'an) odziwa mwa 
ana A Israeli? (Kotero kuti ena 
alowa M'Chisilamu). 

198. Ndipo tikadaivumbulutsa 
kwa wina Amene sali Muarabu, 












Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 I 795 I ^ ^ *>i r n tiyuiJi «jj-* 



199. Kotero kuti 
nkuwawerengera momveka 
Bwino, sakadaikhulupirira. 

200. Momwemo ndimo 
tidalowetsera kuitsutsa (Qur'an) 
m'mitima ya oipa. 

201. Sangaikhulupirire kufikira 
ataona Chilango chowawa. 

202. Ndipo chidzawadzera 
mwadzidzidzi Asakuzindikira; 

203. Adzayamba kunena: "Kodi 
ife tipatsidwa Nthawi (yoti tilape)?" 

204. Kodi akuchifulumizitsa 
chilango Chathu? 

205. Kodi ukuona bwanji, ngati 
Titawasangalatsa zaka 
(zankhaninkhani) 

206. Kenako nkuwadzera 
(chilango) chomwe Adalonjezedwa, 

207. Sizidawathandize zomwe 
Adali kusangalatsidwa nazozo? 

208. Ndipo sitidauononge 
Mudzi uliwonse koma Udali ndi 
achenjezi, 

209. (Kuti akhale) chikumbutso. 
Ndipo Sitidali osalungama 
(powaononga Popanda 
kuwachenjeza). 

210. Ndipo Asatana 
sadaivumbulutse (iyi Qur'an 
monga osakhulupirira Akunenera 
monyoza). 



fei-^^^t 



*]>w 



<%^v$a^^ 



^0S^Z3^&M 



%>g®$$&M 






%&&*$&» 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



796 



1 * frj^rl T 1 tlyuiJl 5jj-- 



211. Ndipo sikoyenera kwa iwo 
(Kuivumbulutsa Qur'an) ndiponso 
sangathe. 

212. Ndithu, iwo 
ngotsekerezedwa Kumvetsera 
(zimene angelo Amalankhula 
kumwamba). 

213. Choncho usapembedze 
mulungu wina Pamodzi ndi 
Mulungu, kuti usakhale Mwa 
olangidwa. 

214. Ndipo achenjeze abale ako 
apafupi, 

215. Ndipo fungatira ndi phiko 
lako amene Akutsata mwa 
okhulupirira.(Ukhale wachifundo 
kwa iwo). 

216. Ngati atakunyoza, nena: 
"Ine ndili Kutali ndi zimene 
Mukuchitazo." 

217. Ndipo tsamira kwa 
(Mbuye wako) Mwini Mphamvu 
zoposa; Wachisoni 

218. Yemwe akukuona pamene 
ukuimirira (Pamapemphero), 

219.Ndikutembenukatembenuka 
kwako (Pogwetsa mphumi yako 
pansi ndi Kudzuka ndikuimirira) 
pamodzi ndi Ogwetsa mphumi 
pansi (polambira Mulungu). 

220. Ndithu, lye Ngwakumva; 
Ngodziwa Chilichonse. 



%s&&*yjii&& 



k£&v$\<£& 






^0€&&'^3 



%&*£&?&£ 






o^Xg&vk 



Surat 26. Ash-Shu'ara Juzu 19 



797 



\ * *j*-l Y 1 *iyuiJl Sjj^ 



221. Kodi ndikuuzeni amene 
asatanaAmawatsikira? 

222. Amamtsikira yense 
wabodza Lamkunkhuniza; 
wamachimo. 

223. Amawaponyera (asatana 
anzawo a mu anthu) Zimene 
azimva. Koma ambiri a iwo 
Ngabodza. 

224. Ndipo alakatuli (olakatula 
zopanda Phindu) amatsatidwa ndi 
(anthu) Opotoka. 

225. Kodi suona kuti iwo 
akungoyumbayumba M'chigwa 
chilichonse (Chamawu)? 

226. Ndithunso, iwo akunena 
zomwe sachita; 

227. Kupatula amene 
akhulupirira Ndikumachita 
zabwino, ndikumamtchula 
Mulungu mowirikiza, 
ndikuzipulumutsa Okha pambuyo 
pochitiridwa zoipa. Ndipo 
posachedwa amene adzichitira 
Okha zoipa adziwa Kotembenukira 
komwe adzatembenukire. 



® 




Surat 27. An-Naml Juzu 19 798 ) ^ ^jA-i t V J^Ji 5jj-- 



Surayi ikufotokoza nkhani ya Musa ndi zozizwitsa zake ndi 
nkhani ya Daudi, ndi kuti Sulaiman adalowa m'malo mwa 
Daudi. Ndipo yafotokozanso kuti ziwanda, anthu ndi mbalame 
zimasonkhanitsidwa ndi kugonjera zofuna za Sulaiman. Ikutinso 
iye amazindikira ziyankhulo za nyama, potero amayamika 
Mulungu kwambiri yemwe adamzindikiritsa ziyankhulozo. 

Surayi yafotokozanso zakusowa kwa mbalame yotchedwa 
Huduhudu ndi kudza kwake ndi nkhani ya Bilikisi yemwe ndi 
anthu ake adali kupembedza dzuwa, komanso Sulaiman atamva 
zimenezo adamtumizira kalata, ndipo Bilikisi pofuna kuyankha 
kalatayo adangotumiza mitulo. Izi zidachitika atakhala upo ndi 
anthu ake. Ndipo yafotokozanso kuti mpando wachifumu wa 
Bilikisi adabwera nawo kwa Sulaimani iye mwini asadadze, 
kupyolera m'mphamvu za wodziwa zam'buku. Komanso surayi 
ikufotokoza nkhani yakulowa kwa Bilikisi m'nyumba ya 
Sulaiman imene idamudabwitsa. 

Surayi yafotokozanso nkhani ya Swaleh pamodzi ndi anthu 
ake, ndi nkhani ya Luti pamodzi ndi anthu ake ndi kuti iye ndi 
banja lake adapulumuka kuchionongeko kupatula anthu oipa. 

Surayi ikudzutsa maganizo athu kuti tiyang'ane zakumwamba 
ndi zapansi pano zomwe zikusonyeza kukhoza ndi mphamvu za 
Mulungu. Ndiponso yafotokoza za ulemerero wa Qur'an; Qur'an 
yomwe ikuitanira ku njira yolunjika. Koma otsutsa akunyozera 
ulaliki wa Qur'an yomwe ikufotokoza kuti m'nthawi yakutha 
dziko lapansi kudzatuluka chinyama chomwe chidzakhala 
chikuwayankhula anthu kuti iwo samatsimikizira zisonyezo za 
Mulungu. Kenako surayi yakumbutsa anthu kuti kudzakhala 
zoopsa lipenga lakutha kwadziko likadzaimbidwa ndi kuti 
nthaka idzagwedezeka zolimba ndipo mapiri adzakhala akuyenda 
monga mitambo. Pomaliza surayi yalangiza Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) njira imene angatsate pa utumiki wake. 



Siirat 27. An-Naml Juzu 19 



799 



S<\ tjir\ 



rv j^JiSj^ 



SuratAl-Naml XXVII 






M'dzina la Mulungu waChifundo 
Chambiri, waChisoni. 

1. Td-Sin. Izi ndi aya (ndime) 
(za Qur'an Buku lodzazidwa ndi 
zothandiza), Ndiponso buku 
lofotokoza (chilichonse Chauzimu 
ndi chamoyo wadziko); 

2. (Qur'an) nchiongoko ndi 
nkhani yabwino Kwa okhulupirira, 

3. Amene akupemphera swala 
(zisanu, Modzichepetsa ndi 
mokwaniritsa malamulo Ake) ndi 
kumapereka zakati (m'nthawi 
yake), Ndipo iwo ali ndi 
chitsimikizo champhamvu Cha 
(moyo wa) tsiku lachimaliziro. 

4. Ndithu, amene sakhulupirira 
za (moyo wa) Tsiku la chimaliziro, 
takometsa kwa iwo Zochita zoipa 
kukhala ngati zabwino; Choncho 
iwo akungoyumbayumba 
(m'kusokera Kwawo). 

5. Iwowo ndiamene adzapeza 
chilango choipa; Iwo tsiku 
lachimaliziro ngotayika zedi, 
(Adzaonongeka kumoto motheratu). 

6. Ndipo ndithu, iwe 
ukuphunzitsidwa Qur'an 
Kuchokera kwa Mwini nzeru 
zakuya, Wodziwa kwambiri. 



mm. 



M 



oj&£\<J£-3^j 



-w 



%l^^^:i^np 















Surat 27. An-NamI Juzu 19 



800 ^ *>» 



tV J-JlSjj^ 



7. (Kumbuka) Musa pamene 
adauza banja lake (Mkazi wake): 
"Ndithu, ine ndaona moto; 
Posachedwapa ndikubweretserani 
nkhani, Zakumeneko kapena 
ndikubweretserani Chikuni 
chamoto kuti inu muothe. 

8. Ndipo pamene adaudzera 
(motowo) Kudaitanidwa: 
"Wadalitsidwa yemwe ali M'moto 
ndi yemwe ali m'mphepete 
mwake; Ndipo walemekezeka 
Mulungu Mbuye wazolengedwa. 

9. E, iwe Musa! Ndithu, ine 
ndine Mulungu, Wamphamvu 
zoposa; Wanzeru zakuya. 

10. Ndipo ponya (pansi) ndodo 
yako! (Pamene adaiponya 
idasanduka njoka), Pamene 
adaiwona ikugwedezeka (ndodo 
ija) Ngati njoka, adatembenuka 
kuthawa, Ndipo sadacheuke 
(kapena kudikira kuti Amve mawu 
omvekawo): "E, iwe Musa! 
Usaope. Ndithu Ine, saopa Kwa 
Ine atumiki. 

11. Koma amene wadzichitira 
yekha zoipa, Kenako nkusintha 
(pochita) zabwino pambuyo Pa 
zoipa, (ndimkhululukira) pakuti 
Ine ndine Wokhululuka kwabasi, 
Wachifundo chambiri. 

12. Ndipo lowetsa dzanja lako 
palisani la mkanjo Wako, ndipo 












by* usjoU*^O^V^(^j)J 



{$9 4f9*t< 9\\< 



9 /('.'"WC Si ,*9- '\" 9 \ *'Y 



Surat 27. An-Naml Juzu 19 



801 



>*\ «.j4-i 



TVj^JlSj^ 



lituluka lili loyera, (kuyera) 
kopanda Matenda. (Ziwirizi) zili 
m'gulu la Zododometsa zisanu ndi 
zinayi. Pita nazo kwa Farawo ndi 
anthu ake; ndithu, iwo ndianthu 
Otuluka m'chilamulo cha Mulungu." 

13. Pamene zidawadzera 
zizindikiro zathu Zosonyeza (kuti 
iye ndimtumiki wa Mulungu) 
adati: "Awa ndimatsenga 
woonekera." 

14. Ndipo adazitsutsa 
(zisonyezozo) mwachinyengo Ndi 
modzikuza chikhalirecho mitima 
yawo Idatsimikiza (kuti ndizoona 
zochokera Kwa Mulungu); 
choncho, yang'ana adali Bwanji 
malekezero a oononga! 

15. Ndipo ndithu, Daudi ndi 
Sulaiman tidawapatsa Nzeru 
(zazikulu; adayamika Mulungu) 
adati: "Kuyamikidwa konse 
kwabwino nkwa Mulungu Yemwe 
watichitira ubwino kuposa Ambiri 
mwa akapolo ake okhulupirira." 

16. Ndipo Sulaiman adalowa 
mmalo mwa Daudi panzeru ndi 
uneneri ndipo (Sulaiman) Adati: 
"E,inu anthu! Ndithu, 
taphunzitsidwa (Mpaka tikudziwa) 
chiyankhulo cha mbalame, 
Ndiponso tapatsidwa chilichonse; 
ndithu, Umenewu ndiufulu 
wopenyeka. 



9 -»< 


















Surat 27. An-Naml Juzu 19 



802 



>* *>i 



XV J^JlSj^ 



17. Ndipo adasonkhanitsidwa 
kwa Sulaiman Ankhondo ake 
ochokera m'ziwanda, anthu Ndi 
mbalame,ndipo adawandandika 
M ' magulumagulu, 

18. Kufikira pamene adadza 
pachigwa chanyerere, Nyerere 
idanena (kuuza zinzake): "E, inu 
Nyerere, lowani m'nyumba zanu 
poopa kuti Angakupondeni 
Sulaiman ndi magulu ake 
Ankhondo pomwe iwo sakudziwa 
(za inu)." 

19. Ndipo adamwetulira, 
kuseka, chifukwa cha Mawu ake 
aja (mawu a nyerere); ndipo 
(Sulaiman) adati: "E, Mbuye 
wanga! Ndipatseni nyonga zakuti 
ndizithokozera Mtendere wanu 
umene mwandidalitsa nawo 
Pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti 
Ndizichita zabwino (zomwe) 
mukuziyanja; Kupyolera 
m'chifundo chanu, ndiponso 
Ndilowetseni m'gulu la akapolo 
anu abwino." 

20. Ndipo adayamba kuyendera 
Mbalame, adati: "Kodi bwanji 
Sindikumuona Huduhudu? Kapena 
ali m'gulu la Amene pano palibe? 

21. "Ndithu, ndithu, 
ndimulanga chilango Chokhwima, 
kapena ndimzinga (ndimdula 
Khosi) pokhapokha andibweretsere 















S^&ajssgagi 



Siirat 27. An-Naml Juzu 19 



803 



H *>< 



YV J^JlSjj- 



umboni Womveka (wosonyeza 
kuti adachoka Pazifukwa 
zomveka)." 

22. Ndipo (Huduhudu) 
sadakhalitse nthawi Yaitali; ndipo 
adati (kwa Sulaiman): 
"Ndatulukira zomwe iwe 
sudazitulukire, Ndipo 
ndakubweretsera nkhani 
yotsimikizika Kuchokera ku Saba. 

23. Ndithu, ine ndapeza mkazi 
akuwalamulira (Anthu akudziko la 
Saba), ndipo wapatsidwa 
Chilichonse; ndipo ali ndi 
chimpando Chachikulu chachifumu. 

24. Ndampeza iye ndi anthu ake 
akulambira Dzuwa kusiya 
Mulungu; ndipo Satana 
Wawakometsera zochita Zawo 
zoipa; choncho wawatsekereza 
Kunjira yolungama, tero 
Sadaongoke. 

25. Kuti asamlambire Mulungu 
yemwe Amatulutsa zobisika 
kumwamba ndi pansi; Ndipo 
akudziwa zimene mukubisa ndi 
zimene Muonetsa poyera. 

26. Mulungu! Palibe wina 
wopembedzedwa Mwachoona 
koma Iye basi; Mbuye wa Mpando 
Waukulu." 

27. (Sulaiman) adati "Tiona 
ngati wanena Zoona kapena (ngati) 
uli m'gulu laonama. 












{^^^(Mo^^^ijS 



Surat 27. An-Naml Juzu 19 



804 I 1 * ^>» 



rvj^Jioj^ 



28. Pita ndi kalata yangayi, 
kaiponye kwa iwo; Kenako 
ukadzipatule kwa iwo (ukakhale 
Pambali) ndi kuona momwe 
azikayankhira." 

29. (Mfumukazi) idati: "E, inu 

nduna! Ndithu, Kalata 
yolemekezeka Yaponyedwa kwa 
ine. 

30. Yachokera kwa Sulaiman, 
ndipo mawu ake Ndi awa: M'dzina 
la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni. 

31. Musadzikweze kwa ine, 
Ndipo idzani kwa ine Muli 
ogonjera malamulo anga." 

32. (Mfumukazi idaonjezera) 
kunena: "E, inu, Nduna! 
Ndilangizeni pankhani yangayi; 
Sindilamula kanthu mpaka inu 
Mutandibwerera." 

33. (Nduna) zidati: "Ife ndife 
eni nyonga ndi eni Kumenya 
nkhondo mwaukali; koma zonse 
Zili ndi inu; choncho yang'anani 
mmene Mungalamulire." 

34. (Mfumukazi) idati: "Ndithu 
mafumu Akamalowa m'mudzi (wa 
anthu), Amauononga motheratu, 
ndi kuwachita Olemekezeka 
am'menemo kukhala Onyozeka. 
Mmenemo ndimomwe amachitira 
(Nthawi zonse). 






k&^&ffiM 









Surat 27. An-Naml Juzu 19 



805 



^ fr>* 



rvjuJUj^ 



35. Koma ine nditumiza mitulo 
kwa iwo ndi Kuyembekezera 
zimene abwere nazo 
Otumidwawo." 

36. Pamene adafika 
(wamthenga wamkulu) kwa 
Sulaiman (ndi kupereka mphatso 
zija, Sulaiman adazikana) nati: 
"Mukundithandiza Ndi chuma? 
Zimene Mulungu wandipatsa 
Ndizabwino kuposa zimene 
wakupatsani. Koma inu 
mukusangalala ndi mphatso zanu. 

37. Bwerera (nazo) kwa iwo; 
ndithu, tiwadzera Ndi gulu 
lankhondo lomwe iwo sangathe 
Kulimbana nalo; mtheradi, 
tikawatulutsa M'menemo ali 
onyozeka ndi oyaluka," 

38. (Sulaiman adasonkhanitsa 
nduna zake) Nati: "E, inu nduna! 
Ndani abwere ndi Mpando 
wakewo kwa ine asadandidzere Ali 
ogonja"? 

39. Chiwanda chautambwali 
chidati: "Ine Ndikubweretsera 
chimenecho usadaimirire Pamalo 
ako (oweruzira). Ndipo ndithu, ine 
Pa icho (chimpando) ndine 
wanyonga, Wokhulupirika. 

40. Yemwe adali ndi 
maphunziro (akuya) Am'buku 
adati: "Ine ndikubweretsera 
(Chimpandocho) maso ako 



%K 9> 9? \' 



iW&MS^S^ 



erg"''^' 












Surat 27. An-Naml Juzu 19 



806 



^ *>» 



rv j^JiSjj-- 



asadaphetire (Usadatsinzine ndi 
kupenya)." Pamene Adachiona 
chitakhazikitsidwa patsogolo Pake, 
adati: "Izi nchifukwa cha ufulu Wa 
Mbuye wanga kuti andiyese 
mayeso kodi Ndithokoza kapena 
ndiusuliza (ufulu Wake). Ndipo 
amene akuthokoza ndithu, ubwino 
wa Kuthokozako udzakhala pa iye 
mwini. Ndipo amene akukana 
(mtendere wa Mulungu 
Posathokoza), ndithu, Mbuye 
wanga Ngokhupuka; Waulemu, 
(sasaukira Chilichonse kwa anthu)." 

41. (Sulaiman) adati: 
"Msinthireni (Maonekedwe a) 
mpando wakewo kuti tione Kodi 
auzindikira kapena akhala mwa 
omwe Sazindikira (chinthu). 

42. Choncho pamene 
(mfumukazi) idadza, 
Kudanenedwa: "Kodi mpando 
Wako wachifumu uli ngati uwu?" 
Idati, "Uli ngati umenewu, ndithu, 
ndipo ife Tidapatsidwa kuzindikira 
(Za uneneri wanu) tisadaone 
chozizwitsa Ichi; ndipo, ndithu 
tidadzipereka (kwa Mulungu). 

43. Ndipo (Sulaiman) 
adamuletsa zomwe 
Amazipembedza kusiya Mulungu. 
Ndithu (mfumukaziyo) idali Mwa 
anthu osakhulupirira (Mulungu). 

44. (Mfumukazi ija) idauzidwa 
kuti: "Lowa M'nkhonde la 












%y&?jS\Jfr\V& 



Surat 27. An-Naml Juzu 19 



807 



><\ t&\ 



rv j^JiSj^ 



nyumba" koma pamene Adaliona 
adaliganizira kuti ndidziwe; 
Adakweza nsalu kumiyendo yake. 
(Sulaiman) Adati: "Ndithu, 
limeneli ndinkhonde lomwe 
Laziridwa ndi magalasi." 
(Mfumukazi) Idati: "E, Mbuye 
wanga! Ndadzichitira Ndekha 
chinyengo; choncho, ndagonjera 
Kwa Mulungu, Mbuye 
wazolengedwa Pamodzi ndi 
Sulaiman." 

45. Ndipo ndithu,Asamudu 
tidawatumizira M'bale wawo 
Swaleh kuti awauze: 
"Mpembedzeni Mulungu".Choncho 
adali Magulu awiri omwe 
amakangana.(Ena adam'tsata 
Pomwe ena adam'kana). 

46. (Swaleh) adati: "E, inu 
anthu anga chifukwa Ninji inu 
mukufulumizitsa choipa (kuti 
Chidze) musanachite chabwino? 
Bwanji Simukupempha 
chikhululuko kwa Mulungu Kuti 
muchitiridwe chifundo?" 

47. (I wo) adati: "Tapeza 
masoka oipa chifukwa Cha iwe ndi 
omwe uli nawo." (lye) adati: 
"Tsoka lanu lili kwa Mulungu 
(chifukwa cha Zolakwa zanu); 
koma inu ndinu anthu amene 
Mukuyesedwa (ndi Mulungu kuti 
aone ngati Mutsatire Mtumiki 
wake kapena simutsatira)". 


















Siirat 27. An-Naml Juzu 19 



808 



H *>t 



YV J^JlSjj- 



48. Ndipo m'mudzimo adalipo 
anthu asanu ndi Anayi omwe 
amaononga padziko, ndipo 
Samakonza (chilichonse koma 
kuchiononga). 

49. (Iwo) adati: "Aliyense wa 
ife alumbire kwa Mulungu (kuti) 
iye (Swaleh) ndi banja lake 
timthira Nkhondo usiku, ndipo 
kenako Timuuza mlowam'malo 
wake (kuti): "Sitidaone 
kuonongeka Kwa m'bale wake; 
Ndithu, ife tikunena zoona." 

50. Ndipo adakonza chiwembu 
ndi kutchera Misampha 
yamphamvu, nafenso tidawatchera 
Misampha yowaononga, iwo 
asakudziwa. 

51. Tsono tayang'ana, kodi 
malekezero Achiwembu chawo 
adali otani! Tidawaononga iwo ndi 
anthu awo onse. 

52. Izo ndinyumba zawo 
(zomwe zasanduka) Mabwinja 
chifukwa cha chinyengo chawo. 
Ndithu, m'zimenezo muli phunziro 
kwa Odziwa. 

53. Ndipo tidawapulumutsa 
amene adakhulupirira Pakuti 
amamuopa Mulungu. 

54. Ndipo (akumbutse nkhani 
ya) Luti pamene Adanena kwa 
anthu ake: "Kodi mukuchita 
Zadama uku inu mukuziona? 


















Siirat 27. An-Naml Juzu 20 



809 



**' 



tVj^JUj^ 



55. Kodi inu mukugona ndi 
amuna pokwaniritsa Chilakolako 
(cha chilengedwe) kusiya Akazi? 
koma inu ndinu mbuli." 

56. Koma anthu ake sadayankhe 
yankho Una Koma ili (lakuti): 
"Apirikitseni otsatira Luti 
M'mudzi mwanumu; ndithu, iwo 
ndianthu Odziyeretsa (asakhale 
Pamodzi ndi ife adama)." 

57. Choncho tidampulumutsa 
iye ndi otsatira Kupatula mkazi 
wake; tidamlingira kukhala 
Mmodzi mwaotsalira (kuti 
aonongedwe Pamodzi ndi 
oonongedwa, chifukwa cha 
Ntchito zake zoipa ngakhale kuti 
adali mkazi Wa mneneri). 

58. Ndipo tidawavumbwitsira 
mvula (yamiyala); Iipirenji mvula 
ya ochenjezedwa (Koma 
osachenjezeka)! 

59. Nena: "Kuyamikidwa konse 
kwabwino nkwa Mulungu, ndipo 
mtendere ukhale pa akapolo Ake 
omwe adawasankha. Kodi 
wabwino Ndi Mulungu kapena 
zimene akumphatikiza Nazozo? 

60. (E, iwe Mtumiki! Pitiriza 
kuwafunsa) Kodi kapena 
(wabwino) ndiamene adalenga 
Thambo ndi nthaka (ndi 
zam'menemo) ndi Kukutsitsirani 
mvula (yothandiza) kuchokera 






&r.; v 









Surat 27. An-NamI Juzu 20 



810 



*>i 



TV J-J»Sj>-» 



Kumwamba,choncho ndi madziwo 
Timameretsa madimba okongola. 
Inu Simungathe kumeretsa 
mitengo yake. Kodi Pamodzi ndi 
Mulungu pali mulungu (wina)? 
Koma iwo (Akafiri) ndi anthu 
opotoka. 

61. Kodi kapena (wabwino) 
ndiamene adapanga Nthaka 
kukhala malo okhazikika ndi kuika 
Mitsinje pakati pake ndi 
kuipangira mapiri, Ndi kuika 
chitsekerezo pakati panyanja 
Ziwiri (nyanja yamadzi amchere, 
ndi yamadzi Ozizira)? Kodi 
pamodzi ndi Mulungu pali 
Mulungu wina? Koma ambiri a 
iwo sadziwa. 

62. Kapena (wabwino) 
ndiyemwe amamuyankha 
Wozunzika akamampempha ndi 
kumchotsera Masautso ake ndi 
kukuchitani inu kukhala Oyendetsa 
dziko lapansi? Kodi pamodzi ndi 
Mulungu pali mulungu wina? 
Ndithu, kulangika kwanu nkochepa. 

63. Kapena (wabwino) 
ndiyemwe Amakuongolerani 
mumdima wapamtunda Ndi 
panyanja ndi kutumiza mphepo 
kuti Ikudzetsereni nkhani yabwino 
patsogolo Pa chifundo chake 
(mvula isanagwe)? Kodi pamodzi 
ndi Mulungu pali mulungu Wina? 
Mulungu watukuka Kuzimene 
akumuphatikiza nazo. 















Surat 27. An-Naml Juzu 20 



811 



*>' 



TV J^Jtojj- 



64. Kapena (wabwino) ndiamene 
adayambitsa Zolengedwa, (ndipo) 
kenako adzazibweza, Kapenanso 
amene amakupatsani riziki 
(Chakudya) kuchokera 
kumwamba ndi M'nthaka? Kodi 
pamodzi ndi Mulungu pali 
Mulungu winanso? Nena: 
"Bweretsani Umboni wanu ngati 
mukunena zoona (Wotsimikizira 
kuti Mulungu ali Ndi mnzake)". 

65. Nena: "Palibe amene alipo 
kumwamba ndi Pansi akudziwa 
zam'seri (zomwe zisanadze) 
Kupatula Mulungu basi. Ndipo 
(amene Akuwapembedza) sadziwa 
kuti nliti Adzaukitsidwa ku imfa. 

66. Kwakhwima liti kudziwa 
kwawo (Zakudza) kwa tsiku la 
chimaliziro? Koma iwo ali 
mchikaiko ndi za tsikulo; Koma 
iwo ngakhungu pazatsikulo. 

67. Ndipo adanena omwe 
adatsutsa (za Mulungu): "Kodi 
tikadzakhala dothi, ife ndi makolo 
athu Akale, (nzoona) 
tidzatulutsidwanso (M'manda tili 
amoyo)? 

68. Ndithu, tidalonjezedwa izi, 
ife ndi makolo Athu kale, izi 
sichina koma ndi nthano (Zabodza) 
za anthu akale." 

69. Nena: "Yendani padziko Ndi 
kuona momwe adalili mapeto a oipa". 


















\&? v>J V )3 (y^VjUh Genual 



Siirat 27. An-Naml Juzu 20 812 Y • *jk-\ 



rvjuJiajj-- 



70. Ndipo usawadandaulire, 
ndiponso usakhale Wobanika 
chifukwa cha ziwembu zomwe 
Akuchita. 

71. Ndipo (iwo) akuti: "Kodi 
lonjezoli Lidzachitika liti, ngati 
Mukunena zoona?" 

72. Nena: "Kapena zina mwa 
zomwe Mukuzifulumizitsa zili 
Pafupi kukupezani." 

73. Ndipo, ndithu, Mbuye wako 
ndi mwini Kupereka ufulu 
(waukulu) kwa anthu; koma 
Ambiri a iwo sathokoza. 

74. Ndipo ndithu, Mbuye wako 
akudziwa zomwe Zikubisa zifuwa 
zawo ndi zomwe Akuonetsera 
poyera. 

75. Ndiponso palibe chobisika 
kumwamba ndi M'nthaka koma 
chili m'buku lofotokoza Chilichonse. 

76. Ndithu, Qui*' an iyi, 
ikufotokoza kwambiri Za ana a 
Israeli pazambiri zomwe iwo 
Akutsutsana. 

77. Ndipo ndithu, iyi (Qur'an) 
ndichiongoko ndi Chifundo kwa 
okhulupirira. 

78. Ndithu, Mbuye wako 
adzalamula pakati Pawo ndi 
chiweruzo chake (choona); ndipo 
lye Ngwamphamvu zoposa 
Ngodziwa Chilichonse. 






©tw: 



?>>\*?s 






fit'/ 9 I *»"\\\< \ l' s*\>l- 



•s' 









Surat 27. An-Naml Juzu 20 



813 



Y* ij±\ 



TV JuJidj^- 



79. Choncho tsamira kwa 
Mulungu; ndithu, iwe uli panjira 
Yachoonadi yoonekera. 

80. Ndithu,iwe sungathe 
kuwachititsa kuti amve Kuitana 
kwako akufa, ndiponso sungathe 
Kuwachititsa kuti agonthi amve 
kuitanako, Pamene akucheuka 
kutembenuza misana (Osafuna 
kumva ulaliki wako). 

81. Ndiponso suli owaongola 
akhungu M'kusokera kwawo, 
ndipo sungachititse Kuti amve 
(uthenga wako) kupatula yemwe 
Akukhulupirira aya (ndime) Zathu; 
iwowo Ndiwo ogonjera malamulo 
(Athu). 

82. Ndipo mawu (onena Kudza 
kwa Kiyama) Akadzatsimikizika 
pa iwo, Tidzawatulutsira nyama 
m'nthaka imene Idzawayankhula 
kuti ndithu, anthu adalibe 
Chitsimikizo pa aya (ndime) Zathu. 

83. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
lomwe Tidzasonkhanitsa 
magulumagulu Mum'badwo 
uliwonse omwe amatsutsa Aya 
(ndime) Zathu. Ndipo Iwo 
adzakhala magulumagulu. 

84. Kufikira pomwe adzaza; 
(Mulungu) adzati: "Kodi inu 
mudazitsutsa aya (ndime) Zanga 
Popanda kuzidziwa bwinobwino, 
Nanga mumachita chiyani?" 















Siirat 27. An-Naml Juzu 20 



814 



*>> 



TV J^Jl 5jj-- 



85. Ndipo mawu onena za 
kuonongeka Adzatsimikizika pa 
iwo, chifukwa cha Chinyengo 
chawo (chodzichitira okha) Ndipo 
iwo sadzawiringula. 

86. Kodi saona kuti Ife tapanga 
usiku ndi Cholinga chakuti 
apumule m'menemo, Ndinso usana 
woyera (kuti aone)? Ndithu Mu 
zimenezo muli zizindikiro Kwa 
anthu okhulupirira. 

87. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
limene lipenga (La chiweruzo) 
lidzaimbidwa, Adzadzidzimuka 
amene ali kumwamba Ndi amene 
ali pansi kupatula yemwe Mulungu 
wamfuna (kuti Asayumbeyumbe); 
ndipo onse Adzam'dzera (Mulungu) 
ali odzichepetsa (Ofooka). 

88. Ndipo ukuona mapiri ndi 
kuwaganizira kuti Akhazikika 
pomwe akuyenda kuyenda kwa 
Mitambo. Chimenecho 
ndichikonzero cha Mulungu 
chimene adakonzera chinthu 
Chilichonse. Ndithu Mulungu 
akudziwa Zonse zimene muchita. 

89. Amene adzaza ndi 
chabwino, adzalandira Mphoto 
yoposa chabwinocho; Ndikuopsa 
kwa tsiku limenelo, Iwo adzakhala 
nako mwamtendere. 

90. Koma amene adzaza ndi 
choipa, Adzaponyedwa kumoto 





















&zm$®v%&> 



Surat 27. An-Naml Juzu 20 



815 I T * *>» 



YV J*Jl5j>* 



champhumi, "Kodi mulipidwa 
(china) Osati zomwe mumachita?" 

91. Ndithu, ndalamulidwa 
kumpembedza Mbuye wa mzinda 
uwu, yemwe Adaukhazika 
wopatulika. Ndipo Zinthu zonse 
nza lye (Mulungu), ndipo 
Ndalamulidwa kukhala mmodzi 
Wa ogonjera (Mulungu), 

92. Ndiponso (ndalamulidwa) 
kuti ndiwerenge Qur'an; ndipo 
amene waongoka, ubwino 
Wakuongokako uli pa iye; ndipo 
amene Wasokera, (wadzisokeretsa 
yekha). Nena: "Ndithu, ine 
sikanthu koma ndine mmodzi Wa 
achenjezi. (ndilibe udindo wina 
Woposa uwu)." 

93. Ndipo nena: "Kuyamikidwa 
konse (kwabwino) Nkwa 
Mulungu; posachedwapa 
akusonyezani Zizindikiro Zake, 
ndipo muzizindikira". Ndipo 
Mbuye wako sali wamphwayi ndi 
Zimene mukuchita. 













Siirat 28. Al-Qasas Juzu 20 816 * % frj*-' * A ^a^Ji s^ 




ikufotokoza mwatsatanetsatane nkhani ya Musa 
kuyambira pamene adabadwa, m'nthawi ya ufumu wa Farawo. 
Ndipo panthawiyo Farawo amapha ana achimuna a ma Isiraeli 
poopera kuti mwa iwo mungadzatuluke Mneneri amene 
angathetse ufumu wake. Koma mwa mphamvu za Mulungu, 
Musa sadaphedwe. Ndipo m'malo mwake adaleredwa mnyumba 
ya Farawo mpaka pamene adachoka ku Iguputo mothawa kupita 
ku Madiyani ku Shamu. Kenako adabwera ali ndi mkazi wake 
Binti Shuaibu (AS). 

Ali m'njira kubwerera ku Iguputo, Mulungu adayankhula 
naye. Ndipo adarrisankha kuti asenze Uthenga wa Mulungu. 
Uthengawo adausenzadi. Ndipo pakati pa iye ndi Farawo ndi 
amatsenga a Farawo padapezeka zopezeka mpaka Mulungu 
adawamiza m'nyanja asirikali a Farawo pamodzi ndi iye mwini 
Farawo pomwe Musa ndi ana a Isiraeli adapulumuka. 

Kenako padapezeka nkhani zokhumudwitsa zomwe 
zimachitika pakati pa Musa, Haruna ndi ana a Israeli, omwe 
chikhalidwe chawo sichidali kufuna kugonjera Malamulo a 
Mulungu, monga Karuna ndi ena ambiri onga iye. 




Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



817 



t * sj£-l Y A jfi < / *j & \ 5j^» 



Sural Al-Qasas XXVIII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Td-Sin-Mim. 

2. Izi ndi aya (ndime) za 
m'buku (la Qur'an) Lofotokoza 
(chilichonse chofunika pa Dini). 

3. Tikukulakatulira (iwe 
Mtumiki) nkhani Za Musa ndi 
Farawo m'njira yoona kwa Anthu 
okhulupirira. (Koma 
osakhulupirira Sangapindule 
kanthu ndi nkhanizi). 

4. Ndithu, Farawo adadzikuza 
padziko, ndipo Adawakhazika 
(anthu a m'dzikolo) 
M'magulumagulu; gulu lina la 
mwa iwo Adalifooketsa (poliyesa 
akapolo) ndi kupha Ana awo 
achimuna, ndi kuwasiya a moyo 
Ana awo achikazi. Ndithu, iye 
adali Mmodzi wa oononga 
kwambiri. 1 

5. Ndipo tidafuna kuwachitira 
zabwino amene Adafooketsedwa 
padziko (la Iguputo), ndi 
Kuwachita kukhala atsogoleri ndi 



w. 






ofa$\<£&\&\jr 



-^ 












Farawo adauzidwa ndi mlosi kuti kudzabadwa mwana mwa Aisraeli 
wamwamuna.yemwe adzathetsa ufumu wake. Pamene adamva izi adalamula 
kuti makanda onse a amuna A Israeli aphedwe. Ghoncho ana amuna 
ongobadwa kumene amaphedwa. 



Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



818 



*j*- 1 



V A jflrfeU 3jj-» 



Kuwachitanso kukhala Amlowa 
m'malo ( a Baiti Makadasi). 1 

6. Ndi kuwapatsa mphamvu za 
padziko (kuti Azichita mmene 
angafunire) ndi kuti Timuonetse 
Farawo ndi Hamana ndi magulu 
Awo ankhondo, zomwe amaziwopa 
(kuti Zingawathetsere ufumu wawo). 

7. Ndipo tidamzindikiritsa mayi 
wa Musa ( tinati), "Muyamwitse 
(mwana wako), ndipo Ukamuopera 
(chiwembu cha Farawo), Mponye 
mumtsinje; usaope ndipo 
Usadandaule ndithu Ife 
tidzamubwezera Kwa iwe, ndipo 
tidzamchita kukhala Mmodzi wa 
Atumiki". 

8. Choncho adamtola anthu A 
Farawo kuti mapeto ake Adzakhale 
m'dani kwa iwo ndi Odandaulitsa. 
Ndithu, Farawo ndi Hamana ndi 
magulu Awo ankhondo adali olakwa. 

9. Ndipo mkazi wa Farawo 
adati: "Musamuphe, akhale 
chotsangalatsa diso Langa ndi 
lako; usamuphe mwina 
Angatithandize, kapena 
tingam'chite kukhala Mwana 
(wathu". Adanena izi) uku iwo 
Asakudziwa (kuti adzakhala 
m'dani wawo); 















1 Chimene Mulungu wafuna chimachitika ngakhaie anthu atayesetsa m'njira 
izi ndi izi kuti achizembe. 



Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



819 



*>' 



V A jfl , /i& \ 0jj~* 



10. Ndipo mumtima mwa mayi 
wa Musa Mudali mopanda kanthu 
(mudalibe Maganizo ena koma 
maganizo a Mwana wake). 
Padatsala pang'ono Kuti aonetse 
(chinsinsi cha mwanayo Ponena 
kuti adali mwana wake), 
Tikadapanda kulimbikitsa mtima 
Wake, kuti akhale mmodzi mwa 
Okhulupirira (lonjezo la Mulungu). 

11. Ndipo (mayi wa Musayo) 
adauza Mlongo wake (wa Musa), 
"Mtsatire, (Komwe madzi akupita 
naye)." Choncho iye 
ankamuyang'ana Chapatali pomwe 
iwo samadziwa (Za ichi). 

12. Ndipo poyamba tidamuletsa 
kuti Asayamwe kumawere a 
woyamwitsa, (Kufikira pomwe 
mlongo wake) adati: "Kodi 
ndikusonyezeni eni nyumba Omwe 
angakulerereni ndi kukhala Naye 
momteteza bwino mwanayo?" 

13. Choncho tidamubwezera 
kwa mayi Wake kuti maso ake 
atonthole, (Mtima wake 
ukhazikike) ndi kuti Asadandaule; 
ndi kuti adziwe kuti Lonjezo la 
Mulungu ndi loona. Koma ambiri 
a iwo sadziwa. 

14. Ndipo (Musa) pamene 
adakula Msinkhu wake ndi 
kulingana bwino Tidampatsa nzeru 
ndi maphunziro. Ndipo umo 






riS '»» VCi '\<> >•> '1 












Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



820 



•J*" 1 



t A j tf. ^ 1 Ojj^ 



ndimomwe timalipirira Ochita 
zabwino. 

15. Ndipo (tsiku lina) adalowa 
mumzinda Mozemba, eni 
m'zindawo osadziwa. Ndipo 
adapeza m'menemo anthu awiri 
Akumenyana, mmodzi wochokera 
kugulu Lake, ndipo winayo 
wochokera kwa adani Ake. Tsono 
wakugulu lake uja Adampempha 
chithandizo pa mdani wake uja, 
Ndipo Musa adammenya 
chibagera mpaka Kumupha 
(mdaniyo). Adanena: "Iyi 
(Ndachitayi) ndintchito ya satana; 
ndithu, lye ndimdani 
wosokeretsa,woonekera." 

16. Adati: "E, Mbuye wanga! 
Ndithu Ndadzichitira zoipa 
ndekha! Choncho 
Ndikhululukireni!" Tero 
(Mulungu) Adamkhululukira 
(chifukwa sadalinge Kupha). 
Ndithu, lye (Mulungu) 
Ngokhululuka, Ngwachisoni. 

17. Adati: "O, Mbuye wanga! 
Chifukwa cha kuti mwandidalitsa, 
sindidzakhala Mthangati wa oipa. 

18. Choncho kudamuchera mu 
mzindamo (m'mawa Mwake)uku 
ali wodzazidwa ndi mantha 
Akuyembekezera (kuti chiyani 
chimpeze Pa zimene zidachitika) 
pompo munthu uja Adampempha 









&Jft$ fjp£*$tyy)$* 



"■ -""Si 






Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



821 



*>' 



t A jA^fliil 9jj~i 



dzulo chithandizo ankamuitana 
(Kuti amthandize kumenyana ndi 
m'dani wake Wina). Musa 
adamuuza; ndithudi ndiwe 
Wopotoka owonekera. 

19. Choncho pamene adafuna 
kumpanda, Yemwe ndi mdani wa 
awiriwo, (uja Wofuna chithandizo 
kwa Musa adaganiza Kuti Musa 
afuna kuti ampande iye), Ndipo 
adati: "E, iwe Musa! Kodi 
Ukufuna kundipha monga momwe 
Udaphera munthu uja dzulo? Iwe 
sufuna China koma kukhala 
wodzitukumula (Wankhanza) 
padziko, ndipo sukufuna Kukhala 
mmodzi mwa ochita zabwino 
(Oyanjanitsa okangana ndi 
kukonza zinthu). 

20. (Farawo zitamfika 
mphekesera kuti Musa wapha 
munthu pothangata mu Israeli, 
adalamula kuti Musa paliponse 
Pomwe angapezeke, agwidwe ndi 
Kuphedwa ). Choncho munthu 
adadza Akuthamanga kuchokera 
kumalekezero A m'zindawo. 
Adati: "E, iwe Musa! Akuluakulu 
akuchita upo kuti akuphe Choncho 
choka (m'dziko muno); Ndithu, 
ine ndine mmodzi mwa okufunira 
Iwe zabwino, 

21. Ndipo adachoka 
mumzindawo ali woopa Uku 
akuyembekezera (kumpeza choipa 






Si* 






> •«• m. ' '\\^9 *Sl'C'M \' m \" "<"* 



Siirat 28. Al-Qasas Juzu 20 



822 



*>i 



X A u fi. s i&\ 5jj-» 



Kuchokera kwa adani ake). Adati: 
"E, Mbuye wanga! ndipulumutseni 
Kwa anthu ochita zoipa". 

22. Ndipo pamene adalunjika 
(kumka) ku Madiyani adati: 
"Mwina Mbuye Wanga 
andiongolera kunjira yoyenera." 

23. Ndipo pamene adawafika 
madzi a ku Madiyani (pomwe 
anthu kumeneko Ankatungapo 
madzi), adapeza gulu La anthu 
likumwetsa (ziweto zawo), Ndipo 
pambali (pagululo) adapeza akazi 
Awiri akuletsa (ziweto zawo kuti 
Zisapite kukamwa ndi ziweto 
zinazo). (Musa) adati "Kodi 
mwatani? (Bwanji 
Simukuzimwetsa ziweto zanu?) 
Iwo Adati: "Sitingamwetse (ziweto 
zathu) Mpaka abusa atachotsa 
(ziweto zawo, Chifukwa sitingathe 
kulimbana nawo). Ndipo bambo 
wathu ndinkhalamba Yaikulu 
kwabasi." 

24. Choncho (Musa) 
adawamwetsera (ziweto Zawo); 
kenako adapita Pamthunzi, ndipo 
adati: "O, Mbuye wanga! Ndithu, 
Ine ndiwosaukira chabwino 
chimene Munditsitsire." 

25. Kenako mmodzi mwa 
asungwana aja Adadza kwa iye 
uku akuyenda mwamanyazi. 
(Msungwanayo) adati: "Ndithu 



&JS&3& 






\J* I £-*U 6&$ &JX* 'X* *J5 WJ 

<&4 









Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



823 



*>-i 



t A jfl < fl ' d \ 0jj-*» 



tate Wanga akukuitana kuti 
akakupatse malipiro 
Pakutimwetsera (ziweto zathu)." 
Choncho Pamene adamdzera, 
(mneneri Shuaibu) 
Ndikumulongosolera nkhani adati: 
"Usaope; Wapulumuka kwa anthu 
oipa." 

26. Mmodzi wa iwo 
(asungwana aja) adanena: "E, 
bambo wanga mulembeni ntchito 
(Kuti akhale woweta ziweto 
m'malo Mwa ife). Ndithu amene 
alibwino kuti Mumulembe ntchito 
ndi yemwe ali wa-Mphamvu 
wokhulupirika (zonse ziwiri Mwa 
iyeyu zirimo.) 

27. (Shuaibu) adati (kwa iye): 
"Ine Ndikufuna kukukwatitsa 
mmodzi mwa Asungwana anga 
awiriwa, chiongo chake 
Ndikundigwirira ntchito zaka 
zisanu ndi Zitatu; ngati 
utakwaniritsa zaka khumi ndiye 
Kuti nkufuna kwako. Sindikufuna 
kukuvutitsa (Pokuchulukitsira 
zaka); undipeza, Mulungu 
Akafuna, kuti ndine mmodzi wa 
anthu abwino, (Wokwaniritsa 
lonjezo)." 

28. (Musa) adati: "Zimene 
mwandilonjezazi Zili pakati pa ine 
ndi inu. Nyengo iriyonse imene 
ndikwaniritse Pa ziwirizi (pogwira 
ntchitoyo, ndiye Kuti 















®t&& 



Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



824 



Y ♦ s-ji-1 Y A j^-Aflii Oj^t 



ndakwaniritsa lonjezo lanu) 
Musandichitire mtopola. Ndipo 
Mulungu Ndiye muyang'aniri pa 
zomwe tikukambazi. 

29. Musa pamene adakwaniritsa 
nyengoyo, adanyamuka ndi banja 
lake (kubwerera Kwao) adaona 
moto kumbali ya phiri. Adauza 
banja lake: "Dikirani ndithudi ine 
Ndaona moto mwina mwake 
Ndingakutengereni nkhani za 
kumeneko Kapena chikuni cha 
moto kuti muothe". 

30. Tsono pamene adaudzera, 
adaitanidwa Kuchokera mbali ya 
kumanja ya Chigwacho, pa malo 
wodalitsidwa Kuchokera mu 
mtengo ankati: "E, Iwe Musa 
ndithudi Ine ndi Mulungu Mbuye 
wazolengedwa." 

31. Ndipo ponya (pansi) ndodo 
yakoyo! Choncho pamene 
adayiona Ikugwedezeka monga 
kuti iyo Ndi njoka, adatembenuka 
kuthawa Ndipo sadachewuke. 
(Adauzidwa): "E, iwe Musa! 
Bwera kuno, usaope. Ndithu, Iwe 
ndiwe mmodzi wokhala ndi 
mtendere. 

32. Lowetsa mkono wako 
m'thumba mwako (Palisani la 
mkanjo wako), utuluka Uli 
woyera, popanda choipa. Ukachita 
Mantha, fumbata dzanja Lako 















Surat 28. AI-Qasas Juzu 20 



825 



*>' 



YA ^/^fliJt °JJ-** 



chakukhwapa; (ukatero Mantha 
akuchokera). Izi zidzakhala 
Zizindikiro ziwiri zochokera Kwa 
Mbuye wako kwa Farawo ndi 
nduna Zake. Ndithu, iwo ndianthu 
olakwa". 

33. (Musa) adanena (Moopa) 
"E, Mbuye Wanga! Ine ndidapha 
munthu mwa iwo, Ndipo ndikuopa 
kuti akandipha. 

34. Ndipo m'bale wanga 
(Haaruni) Ndikatswiri 
pakuyankhula kuposa ine. 
Mutumizeni pamodzi ndi ine 
monga Mnthandizi, 
azikandivomereza (pazimene 
Ndizikanena). Ndithu, ine 
ndikuopa Kuti akanditsutsa." 

35. (Mulungu) adati: 
"Tilimbitsa dzanja Lako ndi mbale 
wakoyo ndipo tikupatsani 
Kupambana, iwo sangafikitse 
masautso Pa inu; chifukwa cha 
zozizwitsa Zathuzo. Inu awiri 
ndiamene akutsatireni, ndinu 
Opambana." 

36. Pamene Musa adawadzera 
ndi zizindikiro Zathu zoonekera 
poyera, adati: "Ichi sichina Koma 
ndi matsenga wopeka; sitidamvepo 
Zimenezi kumakolo athu akale." 

37. Ndipo Musa adanena: 
"Mbuye wanga Akumudziwa 
yemwe wadza ndi chiongoko 



©t&>©Gfci*^<3E2 









Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 826 *• *jk* t A j^^\ oj^ 



Kuchokera kwa lye ndi yemwe 
adzakhala Ndi mathero a pokhala 
pabwino. Ndithu,ochita zoipa 
sakapambana". 

38. Ndipo Farawo adati: "E, inu 
nduna (Zanga)! Sindidziwa kuti 
inu muli ndi Mulungu (wina) 
kupatula ine. Choncho, Iwe 
Haamana! Ndiwotchere njerwa 
Ndiye undimangire chipilala kuti 
mwina Mwake ndingamsuzumire 
Mulungu wa Musa.Ndithu, Ine 
ndikumganizira kuti Ndi mmodzi 
wa abodza". 

39. Ndipo iye pamodzi ndi 
makamu ake Ankhondo 
adadzitukumula padziko Popanda 
chilungamo ndipo ankaganiza Kuti 
iwo sadzabwezedwa kwa Ife. 

40. Koma tidamulanga ndi 
magulu ake ankhondo Ndi 
kuwaponya m'nyanja; yang'ana, 
kodi Adali bwanji mathero aochita 
zoipa. 

41. Ndipo tidawachita kukhala 
atsogoleri Oitanira (anthu) 
kumoto; ndipo tsiku Lachiweruzo 
(Kiyama) sadzathandizidwa. 

42. Tidawatsatiziranso 
matemberero padziko lino Lapansi. 
Ndipo tsiku la chimaliziro iwo 
Adzakhala oyipitsitsa (ndi 
kuthamangitsidwa Ku chifundo 
cha Mulungu). 



%#^<J^I&\ 















Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



827 



,>» 



T A j^-Aflil 5 jj-- 



43. Ndipo ndithu, Musa 
tidampatsa Buku Pambuyo 
powononga mibadwo yoyamba 
Kuti likhale chiphanulamaso cha 
anthu (kuti Liwaunikire kunjira 
yolungama), ndi kuti Likhale 
chiongoko ndi chifundo kuti Iwo 
akumbukire. 

44. Ndipo iwe sudali mbali 
yakuzambwe (Kwa phiri limenelo) 
pamene tidampatsa Musa lamulo; 
sudalinso mwa amene Adalipo 
(pamalopo). 

45. Koma ife tidaumba 
mibadwo yambiri (Pambuyo pa 
Mneneri Musa) kotero kuti Zaka 
zidapitapo zambiri pakati pawo. 
Ndipo sudakhale nawo anthu a 
Madiyani Ndi kumawawerengera 
aya (ndime) Zathu; Koma ife tidali 
kutuma (atumiki ndi 
Kuwafotokozera zomwe zidachitika 
Patsogolo ndi pambuyo pawo, 
monga Momwe takutumira iwe ndi 
kukudziwitsa Nkhani zakale ndi 
zimene zikudza Pambuyo). 

46. Ndipo sudali kumbali kwa 
phiri la Turi pamene tidamuitana 
(Mneneri Musa). Koma 
(kutumidwa kwako) Ndimtendere 
wochokera kwa Mbuye wako Kuti 
uwachenjeze anthu omwe 
mchenjezi Sadawadzere (mnthawi 
yaitali) iwe usadadze, Kuti 
akumbukire. 






•^ 












Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



828 



*>' 



T A jfl'AJh Ojj-^ 



47. (Ndipo sitikadatuma) koma 
kuti mavuto Akawapeza ochokera 
(kuzoipa) zomwe Atsogoza manja 
awo, amanena: "Mbuye Wathu! 
Bwanji wosatitumizira Mtumiki 
kuti titsate mawu Anu ndi kukhala 
mwa Okhulupirira". 

48. Koma choona pamene 
chidawadzera Kuchokera kwa Ife, 
adati: "Bwanji Sadapatsidwe 
monga zomwe Adapatsidwa 
Musa? (Monga Kutembenuza 
ndodo kukhala njoka, ndi zina 
Zotero)" Kodi kalelo sadazikane 
zomwe Adapatsidwa Musa? 
Nkunena (za Taurati Ndi Qur'an): 
"Ndi matsenga awiri amene 
Akuthandizana." Ndipo adati: 
"Ndithu, Ife tikuwakana onse." 

49. Nena: "Bwerani nalo Buku 
lochokera Kwa Mulungu lomwe 
lili ndi chiongoko Chabwino 
kuposa awiriwa: (Taurati ya 
Mneneri Musa, ndi iyi Qur'an), 
kuti Ndilitsate ngati inu mukunena 
zoona." 

50. Koma ngati sadakuyankhe, 
dziwa kuti Akutsatira zilakolako 
zawo. Kodi Ndani wasokera 
kwambiri kuposa yemwe 
Akutsatira zilakolako zake 
popanda Chiongoko chochokera 
kwa Mulungu? Ndithu, Mulungu 
saongola anthu Odzichitira zoipa. 












Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



829 



t • *j£-l T A ^./iiil 5jj-»» 



51. Ndipo ndithu, tafikitsa 
mawu kwa iwo Mochulukitsa, 
mwatsatanetsatane Kuti iwo 
akumbukire. 

52. Amene tidawapatsa Buku 
kale ili Lisadadze , akulikhulupirira 
ili (Buku la Qur'an). 

53. Ndipo likawerengedwa kwa 
iwo, akuti: "Talikhulupirira; 
ndithu, ichi nchoona Chochokera 
kwa Mbuye wathu; ndithu, Ilo 
lisanadze ife tidali ogonjera 
(Mulungu) 

54. Iwo adzapatsidwa malipiro 
awo kawiri (Chifukwa chotsatira 
Mneneri Musa Ndi Mneneri Isa, 
kale; ndipo tsopano Ndikumtsatira 
Mneneri Muhammad {SAW}) 
Nchifukwa chakuti adapirira; 
amachotsa Choipa (pochita) 
chabwino, ndipo M'zimene 
tawapatsa akupereka chopereka 
(Sadaka). 

55. Ndipo akamva zopanda pake 
amazipewa, ndipo Amati (kwa 
achibwanawo): "Ife tili ndi Zochita 
zathu inunso muli ndi zochita 
zanu, Mtendere ukhale painu. Ife 
sitifuna (kutsutsana) Ndi mbuli." 

56. Ndithu, iwe sungathe 
kumuongola amene Ukumfuna, 
koma Mulungu amuongola Amene 
wamfuna. Ndipo lye akudziwa Za 
amene ali oongoka. 



&\' 9 *<"•■' 



te£$&Q$}^<£$ 



*&& 



^«&^\sj)^^ 



<& 



^^*<0^f^^0<^f 









Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



830 



,j* 



T A jn yii . l t djj-a 



57. Ndipo akunena (akafiri a m' 
Makka, kuuza Mtumiki):"Ngati 
titsatira chiongoko (ichi Chimene 
wadza nacho) pamodzi ndi iwe, 
Tifwambidwa m'dziko lathu 
(potimenya Nkhondo mafuko ena a 
Arabu)."Kodi Sitidawakhazike 
pamalo opatulika ndi Pamtendere 
pomwe zipatso Zamitundumitundu 
zikudza pamenepo Mwaulere 
(monga riziki) zochokera kwa Ife? 
Koma ambiri a iwo sadziwa. 

58. Kodi ndimidzi ingati imene 
tidaiononga Yomwe inkanyadira 
za moyo wawo (Wosavutika ndi 
wodya bwino)! Umo M'malo 
mwawo simudakhalidwebe 
Pambuyo pawo koma mochepa 
basi; Ndipo ife tidalowa chokolo 
m'zimenezi. 

59. Ndipo Mbuye wako sali 
owononga midzi Pokhapokha 
akatuma Mtumiki mumzinda 
wawo Waukulu ndi 
kuwawerengera mawu a m'ndime 
Zathu, (akakana ndi pamene 
timawaononga); Ndiponso sitili 
owononga midzi pokhapokha 
Anthu ake atakhala achinyengo. 

60. Ndipo chilichonse chimene 
mwapatsidwa Nchosangalatsa 
chamoyo wapadziko Ndiponso 
chokometsera chake (chomwe 
Sichikhalira kutha); koma chomwe 
chili Kwa Mulungu ndicho 















§$&$? 



Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 831 t* *jJh YA j^-aaJi *jj~> 



chabwino, Chamuyaya; kodi 
bwanji simukuzindikira? 

61. Kodi munthu yemwe 
tamulonjeza lonjezo Labwino (kuti 
akalowa ku munda Wamtendere) 
kotero kuti iye akakumana Nalo 
(lonjezolo), angafanane ndi yemwe 
Tamsangalatsa ndi zosangalatsa 
zamoyo Wapadziko basi, kenako 
iye nkukhala Mmodzi 
okaponyedwa (kumoto) tsiku La 
chiweruzo (Kiyama)?" 

62. Ndipo (akumbutse) tsiku 
limene (Mulungu) Adzawaitana, 
adzati: "Ali kuti anzanga Aja 
omwe mumanena (kuti 
ndianzanga)? 

63. Adzanena amene mawu 
(onena zachilango) Atsimikizika 
pa iwo: "Mbuye Wathu! Awa 
ndiamene tidawasokeretsa; 
Tidawasokeretsa monga momwe 
Tidasokerera tikudzipatula Ndi 
iwo kwa inu; Samatilambira ife". 

64. Ndipo kudzanenedwa: 
"Itanani aphatikizi Anu;" Choncho 
adzawaitana koma 
Sadzawayankha.Ndipo azawawona 
mavuto (Pa nthawiyo azakhumba) 
akadakhala Oongoka (padziko 
lapansi kotero kuti Akadapeza 
mtendere pa tsiku La chimaliziro). 

65. Ndipo (akumbutse) tsiku 
limene adzawaitana Nkudzati: 






©, 



-..w^jb 


















Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



832 



V • *-j£-1 T A ^n^aS s 5jj-- 



"Kodi mudawayankha chiyani 
Atumiki?" 

66. Basi tsiku limenelo nkhani 
zidzawasowa Choncho iwo 
sadzatha kufunsana. 

67. Koma amene walapa ndi 
kukhulupirira ndi Kuchita ntchito 
zabwino, adzakhala Mwa 
opambana? 

68. Ndipo Mbuye wako 
amalenga chimene wafuna Ndi 
kuchisankha (chimene wafuna). 
Iwo alibe chifuniro. Mulungu 
Wapatukana ndi zonse zochepetsa 
ulemerero Wake, ndipo watukuka 
ku zomwe Akumphatikiza nazo. 

69. Ndiponso Mbuye wako 
akudziwa zimene Zifuwa zawo 
zikubisa (maganizo awo) ndi 
Zimene akuwonetsera (poyera). 

70. Ndipo lye ndi Mulungu; 
palibe Wopembedzedwa 
m'choonadi koma lye. 
Kuyamikidwa konse (kwabwino) 
pachiyambi Ndi kumapeto 
nkwake; ndipo kulamulanso 
Nkwake, ndipo inu 
mudzabwezedwa kwa lye. 

71. Nena: "Tandiuzani ngati 
Mulungu Atakupangirani usiku 
kuti usachoke Mpaka tsiku la 
chiweruzo (Kiyama), Kodi 
ndimulungu wanji osati Mulungu 






» J "\i$v&&z 



j^jy^oi. 



®v$$Z 









Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



833 



Y » tj)r\ Y A j jfl^fll l 5 jj-- 



Amene angakudzetsereni kuunika? 
Kodi Simumva?" 

72. Nena: "Tandiuzani ngati 
Mulungu ataupanga Usana kuti 
usachoke mpaka tsiku la 
Chiweruzo (Kiyama), Kodi ndi 
mulungu wanji Osati Mulungu 
amene angakudzetsereni Usiku 
m'mene mumapumulamo? Kodi 
simuona (chifundo cha Mulungu)? 

73. Ndipo mu chifundo Chake, 
Adakupangirani usiku ndi usana 
kuti Muzipumulamo ndi 
Kufunafuna zabwino Zake 
(masana) kuti muthokoze. 

74. Ndipo tsiku limene 
(Mulungu) adzawaitana Adzati: 
"Ali kuti anzanga aja amene 
Mumati ndimilungu inzanga?" 

75. Ndipo mumpingo uliwonse 
tidzatulutsa Mboni (yawo 
yowaikira umboni), ndipo 
Tidzawauza: "Bwerani ndi umboni 
wanu". Pamenepo adzadziwa kuti 
choonadi ncha Mulungu, ndipo 
zidzawasowa zimene Amapeka 

76. Ndithu,Karuni adali mwa 
anthu a Musa; Koma adazikweza 
kwa iwo,ndipo tidampatsa 
Nkhokwe za chuma zomwe makiyi 
ake Ngolemetsa kagulu ka anthu 
anyonga (Kuwasenza). Anthu ake 
adamuuza: "Usanyade; ndithu, 
Mulungu sakonda Onyada. 












X£?2 









Siirat 28. Al-Qasas Juzu 20 I 834 Y * ^j*-i Y A ja^Ji 5jj^ 



77. Ndipo funafuna, kupyolera 
m'zomwe Mulungu wakupatsa, 
nyumba yabwino Yomaliza, 
usaiwale gawo lako la m'dziko; 
Chita zabwino monga momwe 
Mulungu Wakuchitira zabwino, 
ndipo usafune Kuononga padziko; 
ndithu, Mulungu sakonda 
Oononga." 

78. Adati: "Ndithu, ndapatsidwa 
izi chifukwa Cha kudziwa kwanga 
komwe ndili nako" Kodi iye 
sadadziwe kuti Mulungu 
Adawaononga anthu patsogolo 
pake omwe Adali anyonga 
kwambiri kuposa iye, Komanso 
osonkhanitsa chuma chambiri 
Ndipo oipa sadzafunsidwa 
zolakwa zawo. (Mulungu 
akudziwa zonse za iwo)! 

79. Choncho, adatulukira kwa 
anthu ake (Monyada) uku 
atadzikongoletsa. Amene Akufuna 
moyo wapadziko adanene 
(Mokhumbira): "Kalangaife! 
Tikadapatsidwa Monga 
wapatsidwa Karuna! Ndithu, Iye 
ngodala kwakukulu." 

80. Ndipo amene adapatsidwa 
kuzindikira Adanena: "Tsoka lanu! 
Malipiro a Mulungu ngabwino 
kwa yemwe Wakhulupirira ndi 
kuchita zabwino, (Kuposa izi ali 
nazo Karuni); ndipo 









b 






Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 



835 



,>> 



Y A u a-4&\ o jj-*> 



Sadzapatsidwa zimenezi koma 
okhawo Ali opirira." 

81. Kenako tidamdidimiza 
m'nthaka iye ndi Nyumba yake; 
ndipo adalibe gulu Lililonse 
lomuthangata popikisana ndi 
Mulungu, ndipo sadali 
mwaodzipulumutsa Okha. 

82. Ndipo ankanena amene 
ankalakalaka Ulemerero wake 
dzulo: " E, zoonadi Mulungu 
amamuonjezera chuma amene 
Akumfuna mwa akapolo Ake 
(Chingakhale Ali oipa 
wosayanjidwa ndi Iye) ndipo 
Amamuchepetsera chuma (amene 
wamfuna Kotero ngakhale ali 
woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda 
Mulungu kutimvera chisoni, 
(Mkukhumbira kwathu pazimene 
adampatsa Karuni)akadatikwirira 
m'nthaka. Ha! Zoonadi 
Osakhulupirira Mulungu 
sangapambane". 

83. Nyumba yomalizirayo 
tikawapangira amene Sakufuna 
kuzikweza pa dziko ndi kuononga. 
Ndipo malekezero abwino adzakhala 
A wanthu owopa Mulungu. 

84. Amene achite chabwino, 
adzapeza mphoto Yoposa chimene 
adachitacho ndipo amene Achite 
choipa sadzalipidwa (china chake) 
Koma zoipa zomwezo zimene 
Adali kuzichita. 






®&t£&\<'^\ 









ei&JSfctfSj 






Surat 28. Al-Qasas Juzu 20 836 



*J*-» 



Y A j^uaiJI 5j^» 



85. Ndithudi yemwe 
wakulamula kuitsata Qur'an, 
mwachoonadi adzakubwezera Pa 
malo pobwerera. Nena! "Mbuye 
Wanga ndi yemwe akudziwa 
amene Wadza ndi chiongoko ndi 
yemwe Ali m'kusokera koonekera 
poyera". 

86. Ndipo iwe sudali kulakalaka 
kuti Ungapatsidwe Buku (pamodzi 
ndi uneneri) Koma izi zidachitika 
pa chifundo chochokera Kwa 
Mbuye wako; choncho usakhale 
M'thandizi wa anthu 
osakhulupirira (Mulungu). 

87. Ndipo asakutsekereze 
kutsatira ndime za (Mawu a) 
Mulungu pa mbuyo 
povumbulutsidwa Pa iwe aitanire 
anthu kwa Mbuye wako, Komatu 
usakhale m'gulu la anthu 
Omphatikiza Mulungu ndi mafano 

88. Ndipo usapemphe mulungu 
wina pa modzi Ndi Mulungu. 
Palibe wopembedzedwa 
Mwachoonadi koma lye yekha. 
Chinthu Chilichonse 
chidzaonongeka kupatula Nkhope 
yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) 
Uli kwa lye ndipo kwa lye ndi 
kumene Mudzabwerera nonsenu. 















Surat29.Al-'Ankabut Juzu20 



837 



r * *j*-l 1 S Cj^jj6\ Ojj~- 



Sura iyi idavumbulutsidwa ku Makka. Aya zake zilipo 69. 
Aya 1 mpaka 11 zidavumbulutsidwa ku Madina. Surayi 
yayamba ndi kufotokoza kuti nkofunika kwa okhulupirira 
kuyesedwa mayeso ndi masautso, monga nkhondo, kuti 
chikhulupiriro chawo chikhale chokhwima. Ndipo yalangiza 
munthu kuti achitire zabwino makolo ake ndi kuchita jihadi 
(nkhondo) panjira ya Chauta. Ndiponso yafotokoza za kusiyana 
chikhulupiriro kwa anthu. Ena mwa iwo akungonena chabe kuti 
akhulupirira pomwe mitima yawo siinakhulupirire. 

Surayi yafotokozanso za Mneneri Nuhu ndi khama lake 
poitanira anthu ake kunjira ya Mulungu. Ndipo yafotokozanso 
nkhani ya Luti ndi machitidwe a anthu ake ndi kutsitsidwa kwa 
angelo odzawaononga pa chionongeko chomwe iye ndi mbumba 
yake adapulumuka kupatula mkazi wake. 

M' surayi mukunenedwanso nkhani ya Shuaibu ku Madiyani, 
ndi nkhani ya Hudu ndi Adi, Swaleh ndi Samudi. Ndipo surayi 
yafotokozanso za kunyengedwa kwa Kaaruna, Farawo ndi 
Haamana ndi malekezero azochita zawo. Kenaka yafotokoza 
kuti mapemphero a Amushirikina maziko ake ngofooka kuposa 
nemba (nyumba ya kangaude). Ndipo yati mafanizo amenewa 
akuzindikiridwa ndi okhawo omwe ali ndi nzeru zakuya. Kenako 
Mulungu walamula Mneneri wake kuti asatsutsane ndi eni 
mabuku koma kupyolera m'njira yabwino. Ndipo wafotokozanso 
kuti Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
adali wosadziwa kulemba ndi kuwerenga. Ikutinso, kusadziwa 
kulemba ndi kuwerenga kukusonyeza kuona kwa uthenga wake. 
Ndipo Chauta wafotokozanso za liuma la Amshirikina pakufuna 
kwawo zozizwitsa zimene atha kuzikana zikapezeka, monga 
momwe anthu a Musa adazikanira. Mulungu m' surayi 
wafotokozanso za malipiro a otsutsa, pa tsiku la chimaliziro. 
Ndipo wafotokozanso za moyo watsiku la chimaliziro. Mulungu 
wafotokoza kuti Amushirikina akakhala pamavuto amapempha 
chauta. Koma akakhala pamtendere amamukana Mulungu. 

Kenako walongosola za mtendere umene adawadalitsa nawo 
eni mzinda wa Makka, koma chikhalirecho iwo samuthokoza. 
Komanso walimbikitsa zakuchita jihadi (nkhondo) panjira Yake. 



Surat29.AI-'Ankabut Juzu20 



838 



t • *j£-l t ^ OjXaJl ijj^p 



SuratAl-'AnkabutXXIX 



. jtz?3?S-.sjw-a. ^-^_/, 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1 . v4 lif-Ldm-Mim . 

2. Kodi anthu akuganiza kuti 
azasiyidwa Popanda kuyesedwa 
ndi masautso pakungonena Kuti: 
"Takhulupirira?" (Iyayi, ayenera 
Kuyesedwa ndithu, ndi masautso 
Osiyanasiyana pamatupi pawo ndi 
pachuma Chawo kuti adziwike 
woona ndi Wachiphamaso). 

3. Ndipo ndithu, tidawayesa 
amene adalipo Patsogolo pawo. 
Ndithu, Mulungu awaonetsera 
Poyera amene ali olankhula zoona, 
Ndithu, Mulungu awaonetsera 
Poyera amene ali olankhula 
zabodza. 

4. Kodi amene akuchita zoipa 
akuganiza Kuti atipambana (kotero 
kuti Sitingawalange)? 
Ndichiweruzo Choipa chimene 
akuweruzacho. 

5. Amene akuyembekezera 
kukumana ndi Mulungu,(agwire 
ntchito yabwino pamoyo Wake 
kuti akakumane naye ndi 
zabwino). Ndithu, nthawi ya 
Mulungu (tsiku la Chimaliziro) 
idza (popanda chikaiko). Ndipo 
lye Ngwakumva (zonena za 



^rn&tiw 



ofa&^^j 



-^ 















Surat29.Al-'Ankabut Juzu 20 



839 



Y • *j£-t T ^ Oj-SoOi djj~> 



akapolo Ake), Ngodziwa 
(zachinsinsi chawo). 1 

6. Ndipo amene akuchita khama 
(polimbana ndi Akafiri, kapena 
pogonjetsa mtima wake Kuti 
utsatire malamulo a Mulungu), 
Ndithu, zabwino za khamalo zili 
pa iye Mwini. Ndithu, Mulungu 
siwosaukira Chilichonse kwa 
zolengedwa Zake. 

7. Ndipo amene akhulupirira 
Ndi kumachita zabwino, 
Tidzawafafanizira zoipa zawo, 
ndipo Tidzawalipira zabwino 
kuposa zomwe Amachita. 

8. Ndipo tamulamula munthu 
kuchitira zabwino Makolo ake. 
Koma ngati atakukakamiza 
(Makolo ako) kuti undiphatikize 
Ine Ndi (zinthu zina) zomwe iwe 
sukuzidziwa, Usawamvere. Kwa 
ine ndiko kobwerera Kwanu, ndipo 
ndidzakuuzani zimene Mumachita. 

9. Ndipo amene akhulupirira 
ndi kumachita Zabwino, 
tidzawalowetsa m'gulu la anthu 
Abwino. 



gta^&^JLPVf 6^&J 



Gtt.ltft 'cAi**' 1 









1 Tanthauzo la ndimeyi nkuti amene akuyembekezera kuti akalandire malipiro 
abwino kwa Mulungu, apirire pamoyo wapadziko lapansi polimbika kumvera 
Mulungu mpaka adzakumane ndi Mulungu. Ndithudi, kukumana ndi Mulungu 
kuli pafupi. 

2 Ngati makolo onse awiri atalimbikira ndi mphamvu zawo zonse kuti iwe 
umukane Mulungu, kapena kuti umuphatikize ndi chinthu china chomwe 
nchosayenera kukhala Mulungu, usawamvere pazimenezo, chifukwa chakuti 
palibe kugonjera cholengedwa polakwira Mlengi. 



Surat29.Al-'Ankabut Juzu20 



840 



t ♦ ^j£-» Y ^ O^lyJl fljj-** 



10. Ndipo alipo ena mwa anthu 
omwe akunena, "Takhulupirira 
mwa Mulungu". Koma 
Akavutitsidwa chifukwa cha 
Mulungu, Amawachita masautso a 
anthu monga Chilango cha 
Mulungu, (sapirira; Iwowa ndi 
achinyengo (Amunafikina). Ndipo 
chikadza chipulumutso chochokera 
Kwa Mbuye wako amanena: 
"Ndithu, ife Tidali pamodzi ndi 
inu" (Koma Chikhalirecho 
akunena zonama). Kodi Mulungu 
sadziwa zomwe zili m'zifuwa Za 
zolengedwa? 1 

11. Ndipo ndithu, Mulungu 
awaonetsera Poyera amene 
akhulupirira (moona), Ndiponso 
awaonetsera poyera Amunafikina 
(achinyengo). 

12. Ndipo amene 
sadakhulupirire adanena kwa 
Okhulupirira: "Tsatani njirayathu; 
(Musatsate njira ya Muhammad). 
Ife Tidzakusenzerani machimo anu 
(kuti Chilichonse chisakupezeni). 
Koma Sadzasenza chilichonse cha 
machimo Awo, ndithu, iwo 
ngabodza. 






* ■<'-lS\ft3 h , 



*""7j 









*h;jt 9 '-w-**-< 



Alipo ena pakati pa anthu amene amangonena ndi malirime awo okha kuti: 
"Takhulupirira Mulungu". Koma mmodzi wawo akavutitsidwa chifukwa cha 
chikhulupiriro chakecho, amatuluka m'chipembedzomo. Ndipo masautso a 
anthu amati ndicho chifukwa chomwe chidawachotsetsa m'chipembedzocho. 
Komatu chilango cha Mulungu nchosafanana ndi chilango cha anthu. 
Chofunika kwa iwo nkupirira ndi kulimba mtima; osatekeseka ndi chilichonse 
ngakhale choononga moyo wawo. 



Siirat 29. A1-' Ankabut Juzu 20 



841 



V » tj)r\ V ^ 0^£yJl Sjj-j 



13. Ndipo ndithudi, adzasenza 
mitolo ya machimo Ndi mitolo 
yina yamachimo (ya omwe 
Adawasokeretsa) poiphatikiza 
kumitolo Yawo ya machimo. 
(Nawonso osokezedwa, 
Adzasenzanso mitolo ya machimo 
chifukwa Cha kutsatira kwawo 
anthu owasokezawo). Ndipo pa 
tsiku la Kiyama (chimaliziro,) 
Ndithu, adzafunsidwa pa zimene 
amapeka. 

14. Ndipo ndithu, tidamtuma 
Nuhi kwa anthu Ake ndipo 
adakhala nawo zaka chikwi 
Chimodzi kupatulapo zaka 
makumi Asanu. (Koma m'nthawi 
yonseyi sadatsatire Ulaliki wake). 
Choncho chigumula Chidawapeza. 
(Ndipo adamira onse), Uku ali 
odzichitira zoipa. ] 

15. Tidampulumutsa iye (ndi 
anthu ake) A m'chombo; ndipo 
tidachita ichi kuti Likhale phunziro 
kwa zolengedwa. 

16. Ndipo (akumbutse nkhani 
ya) Ibrahim Pamene adawauza 
anthu ake: "Mpembedzeni 
Mulungu ndi kumuopa. Zimenezo 






'»KtL 









1 M'ndime iyi, Mulungu akumthondoza Mtumiki Wake, Muhammad (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) pomufotokozera kuti kusakhulupirira kwa anthu 
akowa sichinthu chachilendo. Nawonso amene adalipo kale adamtsutsa Nuhi 
ngakhale kuti adalalikira kwa nthawi yayitali mpaka chigumula chidawamiza 
onse. Nawonso anthu akowa aonongedwa monga momwe zidalili ndi anthu a 
Nuhi. Choncho usatekeseke ndi kusakhulupirira kwawo. 



Surat 29. Al-< Ankabut Juzu 20 



842 



Y • tji-l Y ^ O^XjJi 5jj~- 



Nzabwino kwa inu ngati 
mukudziwa (Kusiyana kwa 
chabwino ndi choipa). 

17. Ndithu, inu mukupembedza 
mafano Kusiya (kupembedza) 
Mulungu ndipo Mwadzipangira 
chonama. Ndithu, Amene 
mukuwapembedzawo kusiya 
Mulungu, sangakupatseni riziki 
(madalitso) Funani riziki 
(madalitso) Kwa Mulungu, ndipo 
mpembedzeni lye Yekha ndi 
kumthokoza. Kwa lye ndikomwe 
Mudzabwezedwa (tsiku la 
chimaliziro). 

18. Ndipo ngati mutsutsa, 
ndithu, mibadwo Ya omwe adalipo 
patsogolo panu Idatsutsanso;" 
ndipo kwa Mtumiki Kulibe udindo 
wina koma Kufikitsa uthenga 
woonekera Poyera, (womveka 
bwino). 

19. Kodi saona momwe 
Mulungu ayambitsira Zolengedwa. 
Kenako nkuzibwerezanso. Ndithu, 
kwa Mulungu zimenezo Nzosavuta. 

20. Nena: "Yendani padziko ndi 
kuona momwe Mulungu 
adayambitsira chilengedwe; 
Kenako Mulungu adzaumba, 
kuumba Kwina.Ndithu, Mulungu 
Ndiwokhoza chilichonse. 

21. Amamlanga yemwe 
wamfuna ndipo Amamchitira 



,1| 99 9 * 9 999* * 9 €i 



*'A4XS&#SB&& 









Surat 29. AI-' Ankabut Juzu 20 



843 



t » *j£-l t ^ Oj-£ydl 5jj-» 



chifundo amene wamfuna Ndipo 
kwa lye nonse mudzabwezedwa 

22. Ndipo inu 
simungampambane (Mulungu) 
Padziko ngakhale kumwamba 
(pomuzemba Kuti asakulangeni). 
Inu mulibe mtetezi Kapena 
mpulumutsi kupatula Mulungu". 

23. Ndipo amene akana aya 
(ndime) za Mulungu Ndi 
kukumana Naye amenewo ndiwo 
ataya Mtima pa zakupeza chifundo 
Changa, ndipo Iwowo ndiwo 
adzapeza chilango Chowawa. 

24. Choncho yankho la anthu 
ake silidali lina Koma adangoti: 
"Mupheni kapena mtentheni Ndi 
moto". Koma Mulungu 
adampulumutsa Kumoto. Ndithu, 
m'zimenezi muli Malingalilo 
(osonyeza mphamvu za Mulungu) 
kwa anthu okhulupirira. 

25. Ndipo adanena: "Ndithu, 
inu mwasankha Mafano kukhala 
milungu kusiya Mulungu 
Weniweni, ndipo mukukondana 
pakati panu M'moyo wapadziko; 
(pokhalirana Pamodzi ndi 
kupitiriza kupembedza Mafanowo 
mwachimvano). KomatsikuLa 
Kiyama (chiweruzo), 
mudzakanana Wina ndi mnzake 
ndiponso Mudzatembererana Wina 
ndi mnzake malo anu adzakhala 



«$»W£ 















Surat 29. Al-'Ankabiit Juzu 20 



844 



Y • *jA-l Y S o^ScaJi Ojj-- 



Kumoto, ndipo simudzapeza 
Okupulumutsani 

26. Choncho (Mneneri) Luti 
adamkhulupirira. Ndipo (Mneneri 
Ibrahim) adanena: "Ndithu, Ine 
ndikusamukira (kudziko lomwe) 
Mbuye Wanga (wandilamulira). 
Ndithu, lye Ngwamphamvu 
zoposa Ngwanzeru zakuya." 

27. Ndipo tidampatsa (Mneneri 
Ibrahim) Isihaka ndi Yakubu, 
ndipo Tidaika uneneri ndi Buku pa 
mbumba yake, Ndipo tidampatsa 
malipiro ake padziko Lapansi; 
ndithu iye pa tsiku la chimaliziro 
Adzakhala mwa anthu abwino. 1 

28. Ndipo (akumbutse nkhani 
ya Mneneri) Luti pamene 
adawauza anthu ake: "Ndithu, inu 
mukuchita zadama; palibe Amene 
adakutsogolerani kuzichita 
(Zadamazo) mwa zolengedwa. 

29. Kodi inu mukuchita amuna 
anzanu ukwati Ndi kutseka njira 
(pakuchita chifwamba) Ndi 
kuchita zoipa m'mabwalo anu 
Osonkhanirana?" Koma yankho la 
anthu Ake silidali lina koma 












Ibrahim pamene adasamuka ku Iraki kumka ku palasitina ndi cholinga 
chokafalitsa chipembedzo cha Mulungu kumeneko, Mulungu adamdalitsa ndi 
mwana wotchedwa Isihaka ndi Yakubu mdzukulu wake. Ndipo adasankha 
mbumba yake kukhala mbumba yotulukamo aneneri ndi atumiki. Ndipo mabuku 
akumwamba ankavumbulutsidwa kwa aneneri ochokera m'mbumba yake. 
Mulungu adamuchitira izi chifukwa cha kugonjera malamulo Ake kwathunthu. 



Surat 29. Al-'Ankabut Juzu 20 



845 



T * s-ji-l T ^ Oj-&*Jl 0jj-*> 



kunena kuti: "Tidzere ndi chilango 
cha Mulungucho ngati uli mmodzi 
wa oona". 

30. (lye) adati: "Mbuye wanga 
Ndipulumutseni kwa anthu 
oononga". 

31. Ndipo pamene atumiki athu 
adamdzera Ibrahim ndi nkhani 
yabwino (yoti Abereka Mneneri 
Isihaka), Adanenanso: "Ndithu, 
tiwaononga eni mudzi Uwu; 
ndithu, iwowo ngochimwa." 

32. (Mneneri Ibrahim) 
adayankha: "Koma Mmenemo 
muli Luti". Iwo adati: "Ife ndife 
odziwa kwambiri za omwe Ali 
m'menemo; ndithu, timpulumutsa 
lye ndi banja lake kupatula mkazi 
wake; lye ndi mmodzi wa otsalira 
(woonongeka)". 

33. Ndipo pamene atumiki athu 
adamdzera Luti, Adawadandaulira 
ndi kuwadera nkhawa; (Ndipo 
iwo) adati: "Usaope ndipo 
Usadandaule.Ndithu, ife 
tikupulumutsa ndi Banja lako 
kupatula mkazi wako; iye ndi 
Mmodzi waotsalira (woonongeka)". 

34. "Ndithu, ife tiwatsitsira 
chilango Choipa kuchokera 
kumwamba eni mudzi Uwu 
chifukwa cha kuchimwa kwawo 
(ndi Kuukira malamulo a Mulungu)". 



®^?uA)t 












"W* 






Surat29.Al-'Ankabut Juzu20 



846 



Y • ^£-1 Y ^ o^-SoJl 5jj-- 



35. Ndipo ndithu, tidasiya 
chizindikiro Mmenemo 
choonekera Kwa anthu anzeru. 

36. Ndipo ku Madiyani 
(tidatumako) m'bale Wawo Shuaibu, 
ndipo adati: "E, inu Anthu anga! 
Mpembedzeni Mulungu ndipo 
Opani tsiku lachimaliziro Musanke 
muononga padziko." 

37. Koma adamutsutsa. Ndipo 
kugwedezeka Kwa nthaka 
kudawachotsa moyo wawo, Ndipo 
kudawachera ali gwadegwade 
M'nyumba zawo ( atafa). 

38. Nawonso Adi ndi Asamudu 
(Tidawaononga). Mokhala mwawo 
Mukudziwika kwa inu.Satana 
Adawakometsera zochita zawo 
(Zoipa), ndipo adawatsekereza 
kunjira (Zabwino) chikhalirecho 
adali openya, (Anzeru zawo). 

39. Momwemonso Kaaruni, 
Farawo Ndi Hamana 
(adaonongedwa). Ndithu, 
Adawadzera Musa ndi zozizwitsa, 
(Zooneka) koma adadzikweza pa 
dziko. Komatu sadathe 
kumpambana (Mulungu 
Pomulepheretsa Kuwalanga). 

40. Choncho aliyense wa iwo 
tidamlanga Ndi machimo ake. Ena 
a iwo Tidawatumizira chimphepo 
chamiyala; Ena a iwo 
adachotsedwa moyo ndi Mkuwe; 



-A 



3®3^&3&&> 


















Surat29. Al-'Ankabut Juzu 21 



847 



Y 1 *ji-l T <* O^iCyJl 5jj-» 



ena a iwo tidawadidimiza M'nthaka, 
ndipo ena a iwo tidawamiza 
(M'madzi). Si Mulungu amene 
Adawachitira zoipa, koma 
adadzichitira Okha zoipa. 

41. Fanizo la amene adzipangira 
milungu Yabodza kusiya Mulungu 
weniweni, Lili ngati fanizo la 
kangaude (yemwe) Wadzipangira 
nyumba (kuti imsunge, pomwe 
Nyumbayo siingathe kumsunga 
m'nyengo Yozizira kapena 
yotentha), ndithu, nyumba Yomwe 
ili yofooka kwambiri ndi nyumba 
ya Kangaude, akadakhala akudziwa. 1 

42. Ndithu, Mulungu akudziwa 
kupembedza Kwawo zinthu zina 
kusiya lye, iye Ngwamphamvu 
zoposa, Ngwanzeru zakuya. 

43. Ndipo amenewa ndimafanizo 
(omwe) Tikuwaponyera anthu. 
Sangawazindikire Kupatula odziwa. 

44. Mulungu adalenga thambo 
ndi nthaka Mwachoona; ndithu; 
m'menemo muli Zizindikiro kwa 
okhulupirira. 

45. Werengani zimene 
zavumbulutsidwa Kwa iwe (za) 









1 M'ndime iyi Mulungu akufanizira munthu wopembedza mafano ndicholinga 
choti mafanowo adzimthangata pomudzetsera zabwino ndi kumchotsera 
zoipa, kuti ali ngati kangaude yemwe wamanga nyumba ndi cholinga choti 
imteteze kuchisanu ndi kutentha pomwe nyumbayo njofooka yomwe siingathe 
kumteteza kuchisanu kapena kudzuwa. Izi zili chimodzimodzi ndi wopembedza 
mafano. Mafanowo sangamudzetsere zabwino kapena kumchotsera zoipa. 



Siirat 29. Al-'Ankabiit Juzu 21 



848 



t ^ tji-t Y ^ O^-^jJl djj-- 



m'buku, ndipo pemphera Swala; 
ndithu, swala (ikapempheredwa 
Moyenera) imamtchinjiriza 
(Woipempherayo) kuzinthu zauve 
ndi Zoipa. Ndipo kukumbukira 
Mulungu, Ndi chinthu 
chachikulu.Ndipo Mulungu 
Akudziwa zimene mukuchita. 

46. Ndipo musatsutsane ndi 
anthu a Buku Koma kutsutsana 
kwabwino kupatula Amene achita 
zoipa mwa iwo. Ndipo Nenani: 
"Takhulupirira zomwe 
Zavumbulutsidwa kwa ife ndi 
zomwe Zavumbulutsidwa kwa inu, 
ndipo Mulungu Wathu ndi 
Mulungu wanu ndi M'modzi; 
ndipo ife Ndife ogonjera lye." 

47. Ndipo umo ndimomwe 
Takuvumbulutsira Buku (ili la 
Qur'an). Ndipo amene tidawapatsa 
Buku, (Ili lisadadze,monga Taurat 
ndi Injili), Akulikhulupirira; 
akulikhulupiriranso Ena mwa awa 
(Arabu omwe Sitidawapatse 
Buku). Ndipo sangakane ma Ay a 
athu kupatula osakhulupirira. 

48. Ndipo iwe sumawerenga 
buku lililonse, Ili lisanadze; Ndipo 
sudalilembe ndi Dzanja lako 
lakumanja. Zikadatero Ndiye kuti 
anthu Achabe akadakaikira. l 















1 Akadakhala kuti umawerenga ndi kulemba pamenepo pakadakhala 
poyenera kwa osakhulupirira kukaikira Qur'an. Ndime iyi ikufotokoza 



Siirat 29. A1-' Ankabut Juzu 21 



849 



t WjA-i rs o^-^idj^- 



49. Koma izi ndi aya Zathu 
zoonekera poyera (Zomwe 
nzovomerezeka) m'zifuwa za 
Amene apatsidwa nzeru.Ndipo 
sangazikane Aya (ndime) zathu 
koma achinyengo. 

50. Ndipo akunena: "Kodi 
bwanji sizinatsitsidwe Kwa iye 
zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye 
Wake?" Nena: "Zozizwitsa zili 
kwa Mulungu; Ndipo ine ndine 
mchenjezi woonekera, (Ndilibe 
mphamvu zokudzetserani 
Zozizwitsa koma pokhapo 
Mulungu Atafuna)". 

51. Kodi sizidawakwanire kuti 
Takuvumbulutsira buku (ili) 
lomwe Likuwerengedwa kwa iwo? 
Ndithu, M'zimenezo muli 
chifundo ndi phunziro Kwa anthu 
okhulupirira. 

52. Nena: "Mulungu akukwana 
kukhala mboni Pakati panga ndi 
inu;akudziwa za Kumwamba ndi 
zapansi ndipo amene 
Akukhulupirira zachabe ndi kukana 
Mulungu, iwowo ndiwo otayika. 

53. Ndipo akukupempha kuti 
Chilango chidze mwachangu; 
Kukadapanda kuti kudaikidwa 












k£& 









momveka kuti Mtumiki adali wosadziwa kulemba ndi kuwerenga koma 
adamdzetsera Buku ili lomwe m'kati mwake muli nkhaninso za anthu akale 
ndi zinthu zina zobisika. Choncho umenewu ndi umboni waukulu 
wovomereza kuti iye ndi Mtumikidi wa Mulungu. 



Surat29.Al-'Ankabut Juzu21 



850 



Y ^ ^^*-^ t ^ £Jy&jt\ 5jj^ 



Nthawi yodziwika, chilango 
Chikadawadzera. Ndipo ndithu, 
Chidzawadzera mwadzidzidzi 
Asakudziwa. 

54. Akukupempha kuti chilango 
chidze Mwachangu; ndithu, Jahena 
idzawazinga Osakhulupirira. 

55. Tsiku limene 
chidzawavindikira Chilango 
kuyambira kumwamba mpaka 
Pansi pamiyendo yawo; ndipo 
adzanena: "Lawani (malipiro a) 
zomwe munkachita." 

56. E, inu akapolo Anga amene 
mwakhulupirira! Ndithu, nthaka 
yanga njophanuka; (Mukhoza kupita 
dziko lina ngati m'dziko Lanulo 
simupeza mwayi wopembedza 
Mulungu mokwanira); ndipo Ine 
ndekha Ndipembedzeni. 

57. Chamoyo chilichonse 
Chidzalawa imfa. Kenako 
Mudzabwezedwa kwa Ife. 

58. Ndipo amene akhulupirira 
ndi kumachita Zabwino ndithudi 
tidzawakhazika m'zipinda Za ku 
Munda Wamtendere, momwe 
pansi pake Pakuyenda mitsinje; 
adzakhala m'menemo Muyaya. 
Taonani kukhala bwino malipiro a 
ochita zabwino! 

59. Amene adapirira Ndi 
kusamira kwa Mbuye wawo. 



*uS® 






%£&$&*&$<&& 
%&&&& 









®vM'^&&&>&^\ 



Surat 29. Al-'Ankabut Juzu 21 I 851 I * \ *>» M o^&idi 5j^ 



60. Ndi zamoyo zingati zomwe 
sizidzipezera Riziki lake. Mulungu 
akuzipatsa izo Pamodzi ndi 
inunso.Ndipo lye Ngwakumva; 
Ngodziwa. 

61. Ndipo ngati utawafunsa 
(kuti): "Kodi ndani Adalenga 
thambo ndi nthaka, ndi kugonjetsa 
Dzuwa ndi mwezi? Ndithu anena: 
"Ndi Mulungu". Nanga 
akutembenuzidwira Kuti? 

62. Mulungu amamtambasulira 
riziki amene Wamfuna mwa 
akapolo Ake, ndi Kumchepetsera 
(amene wamfunanso). Ndithu, 
Mulungu Ngodziwa kwambiri Za 
chilichonse. 

63. Ndipo ngati utawafunsa 
(kuti): "Kodi Ndani amene 
akutsitsa madzi kuchokera 
Kumitambo ndi kuiukitsa nthaka 
ndi madziwo Pambuyo pokhala 
yachilala?" Ndithu, anena: "Ndi 
Mulungu." Nena: "Kuyamikidwa 
Konse nkwa Mulungu." Koma 
ambiri a Iwo sazindikira. 

64. Ndipo moyo uwu 
wapadziko lapansi Suli kanthu, 
koma chibwana ndi masewera. 
Ndipo Nyumba ya tsiku la 
chimaliziro, Ndiwo moyo 
weniweni, Akadakhala akudziwa. 

65. Ndipo akakwera m'chombo 
(ndi kukumana Ndi zoopsa), 















£#'«& &»&&&$$ 



Surat 29. Al-'Ankabut Juzu 21 



852 



Y \ *j£-» Y ^ o^-£*)l o jj~> 



amampempha Mulungu 
Modzipereka ndikumuyeretsera 
pempho. Koma akawapulumutsa 
ndi kuwafikitsa Kumtunda, iwo 
amayambanso Kumuphatikiza 
Mulungu ndi mafano. 

66. Posathokoza zimene 
tawapatsa. Aleke Asangalale (ndi 
zoipa zawozo); Posachedwa 
adzadziwa. 

67. Kodi saona kuti dziko lawo 
(mzinda wa Makka) talichita 
kukhala lopatulika, lamtendere 
Pomwe anthu ena 
akutsompholedwa M'mphepete 
mwawo! Kodi akukhulupirira 
Zachabe ndi kuukana Mtendere wa 
Mulungu? 

68. Kodi wachinyengo 
wamkulu ndani woposa Amene 
akupekera bodza Mulungu, kapena 
Kutsutsa choona chikamdzera? 
Kodi si Jahena yomwe idzakhala 
Malo a osakhulupirira? 

69. Ndipo amene akulimbikira 
m'njira yathu, (Polimbana ndi 
satana, ndi mzimu woipa Ndi 
zilakolako zoipa zam'thupi, ndi 
cholinga Chofuna kukondweretsa 
Mulungu) ndithu Tiwaongolera ku 
njira Zathu. Ndipo ndithu, Mulungu 
ali pamodzi ndi ochita zabwino. 















Siirat 30. Ar-Rum Juzu 21 



853 



iw>» r* pj^oj^ 




SURAT AR-RUM XXX 




Surayi yayamba ndi kukamba zakugonja kwa Aroma pankhondo 
yomwe idali pakati pawo ndi Aperezi (Persia). Yafotokozanso kuti 
nawonso Aroma adzagonjetsa adani awowo m'zaka zowerengeka. 
Ndipo zidachitikadi monga momwe Qur'an idafotokozera. 

Ichi chidali chozizwitsa chachikulu chosonyeza kuona kwa 
utumiki wa Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
ndi zimene Qur'an ikufotokoza. 

Komanso Surayi yafotokoza za mkangano womwe uli pakati pa 
chipani cha Mulungu ndi chipani cha Satana. Ndithu, mkangano 
umenewu ngwakalekale. Ndipo malinga kuti choona ndi chonama, 
chabwino ndi choipa zonse zilipo, nkhondo padziko lapansi 
siidzatha. Nkhondo idzapitirira mpaka m'tsogolo chifukwa chakuti 
satana akulimbitsa abwenzi ake ndi athandizi ake kuti azimitse 
dangalira la Chauta, ndi kulimbana ndi ulaliki wa Aneneri. Surayi 
yafotokozanso zisonyezo ndi maumboni osonyeza kupambana kwa 
chonama m'mibadwo yosiyanasiyana. Imeneyi ndiyo njira ya 
Mulungu, ndipo panjira ya Chauta simungapeze kusintha kulikonse. 
Tero choona chiyenera kupambana chonama ngakhale patapita 
nthawi yaitali. 

Surayi yafotokozanso za tsiku lomalizira, ndi mabwerero 
oipa a anthu osakhulupirira pomwe Asilamu adzakhala m'minda 
yamtendere akusangalatsidwa. Oipa adzaponyedwa kuchilango cha 
moto. Ndipo amenewa ndiwo malekezero a anthu osakhulupirira. 

Surayi yafotokozanso zina mwa zisonyezo za chilengedwe 
ndi zisonyezo zobisika zomwe zikulangiza mphamvu ya Mulungu 
yoposa, ndi umodzi Wake; zomwezonso zikusonyeza ukulu ndi 
kutukuka kwa Chauta yemwe nkhope zikumlambira. Ndipo 
yapereka mafanizo osiyanitsa pakati pa amene akupembedza 
Mulungu Wachifundo, ndi omwe akupembedza mafano. 

Surayi yamaliza ndi kufotokoza za akafiri a Achikuraishi 
omwe zisonyezo ndi atetezi sizidawathandize ngakhale kuti 
adaona zizizwa zosiyanasiyana ndi maumboni oonekera poyera. 
Sadalingalire konse; ndipo zonsezi nchifukwa chakuti iwo adali 
ngati akufa.Samamva ndi kupenya komwe. 



Surat 30. Ar-Riim Juzu 21 



854 



Y \ *j*-i 



r • ^ jj)i dj>^ 



Surat Ar-Riim XXX 




M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Alif-Lam-Mim} 

2. Aroma agonjetsedwa (ndi 
Aperezi). 2 

3. M'dziko loyandikira (kwa 
Arabu Lomwe ndi dziko la 
Shamu). Nawonso Pambuyo 



°&&\&&\&w 



J^ 



©5-M 









1 Surayi yayamba ndi zilembo za alifabeti posonyeza kuti Qur'an yalembedwa 
kupyolera m'malemba amenewa omwe Arabu amawayankhula mofewa. 
Koma Akuraishi adalephera kulemba Buku limeneli pomwe malembo ake 
akuwadziwa. 

2 Surayi idapatsidwa dzina loti Rum chifukwa chakuti idalosera kuti Aroma 
adzagonjetsa Aperezi. M'menemo nkuti pamene surayi inkavumbulutsidwa 
ndi kulosera kupambana kwa Aroma iwo adali atagonjetsedwa kale ndi 
Aperezi, kugonjetsedwa zedi kotero kuti maiko awo ambiri adalandidwa ndi 
Apereziwo. Surayi idavumbulutsidwa ku Makka m'chaka chachisanu 
nchimodzi (6) kapena chisanu ndichiwiri (7) Mtumiki asanasamuke. Aroma ndi 
anthu akale zedi; amalamulira maiko ambiri. Mzinda wawo waukulu 
umatchedwa Roma m'dziko la Italy. 

Padali mkangano pakati pamfumu ziwiri: Mfumu ya Aroma ndi Mfumu ya 
Aperezi mkanganowo udayamba m'chaka cha 602 A.D, Ndipo pamene 
adamenyana nkhondo Aperezi adagonjetsa Aroma. Ndipo kupambana kwa 
Aperezi kutamveka m'Makka, Arabu opembedza mafano adakondwa 
kwambiri poti naonso Aperezi adali kupembedza mafano ngati iwo. Arabu 
opembedza mafanowo adati kwa Asilamu ndi Akhrisitu: "Anthu a mabuku 
ngati inu mwagonjetsedwa ndi anzathu opembedza mafano, choncho nafenso 
tikugonjetsani inu Asilamu posachedwa." 

Qur'an idalengeza ndime izi ziwiri zomwe mkati mwake muli ulosi uwiri: Ulosi 
woyamba nkuti m'nyengo yosapyolera zaka zisanu ndi zinayi (9) Aperezi 
adzagonjetsedwa ndi Aroma. Ndipo ulosi wachiwiri ukuti Asilamu 
adzagonjetsa Arabu opembedza mafano amumzinda wa Makka. M'chaka cha 
624. Hirakla, mfumu ya Aroma adagonjetsa mzinda wa Madiyani m'dziko la 
Aperezi. Ndipo m'chaka chomwecho naonso Asilamu omwe adali 313 
adagonjetsa gulu lankhondo la Arabu opembedza mafano omwe kuchuluka 
kwawo kudali 1,000 pankhondo yomwe idachitikira pamalo wotchedwa Badri. 
Ndipo opembedza mafanowo adagonjetsedwa moipa. Potero ulosi umene 
Qur'an idalosera udakwaniritsidwa. Ndipo ichi chidali chinthu chozizwitsa zedi, 
chomwe chimasonyeza kuti Qur'an ndi Mawudi a Mulungu. 



Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



855 



Y> ij±\ 



r * fjj\ ijj~> 



pogonjetsedwa kwawo, 
Adzagonjetsa (Aperezi). 

4. Mzaka zochepa (zosapyolera 
10). Zonse Nza Mulungu, 
pambuyo ndi patsogolo 
(Pankhondoyo). Ndipo tsiku 
limenelo Okhulupirira 
adzasangalala. 

5. Ndi chithandizo cha Mulungu 
(chimene Iwo adzapatsidwa, 
chomwe Ndikugonjetsa Akuraishi 
tsiku Lomwelo). (Mulungu) 
amamthandiza Amene wamfuna, 
ndipo lye Ngwamphamvu zoposa; 
Ngwachisoni. 

6. Hi ndilonjezo la Mulungu 
(loona pa Okhulupirira). Mulungu 
saswa lonjezo Lake. Koma anthu 
ambiri sadziwa. 

7. Akudziwa zoonekera 
(zokhazokha) za Moyo wadziko 
lapansi (zomwe Amadalira 
pamoyo wawo. Monga Ulimi, 
malonda, zomangamanga ndi Zina 
zotero). Ndipo iwo salabadira Za 
tsiku la chimaliziro. 

8. Kodi salingalira mwa iwo 
okha (nkuona Kuti) Mulungu 
sadalenge thambo ndi Nthaka ndi 
zapakati pake, koma 
Mwachilungamo, ndiponso 
kwanthawi Yoikidwa? Ndithu, 
anthu ambiri Ngotsutsa 
zakukumana ndi Mbuye wawo. 



"i^T <iS"l »>\'h ii »< 



©t35Kft Muslin >3f 






Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



856 



n *>i 



r • ?jj\ oj^ 



9. Kodi sadayende pa dziko 
nkuona Momwe adalili malekezero 
a omwe Adaliko patsogolo pawo? 
Adali Anyonga zambiri kuposa 
iwo. Adailima nthaka ndi 
kumangapo Zomangamanga 
kuposa momwe Iwo 
adamangirapo. Ndipo aneneri awo 
Adawadzera ndi zizindikiro 
zoonekera (Koma adawatsutsa, 
ndipo Mulungu Adawawononga). 
Choncho Mulungu sadali 
Owapondereza koma iwo 
ankazipondereza Okha. 

10. Kenako malekezero a 
amene adaipitsa adali Chilango 
choipa kamba koti adakanira Aya 
za Mulungu ndipo Ankazichitira 
chipongwe. 

11. Mulungu ndi Yemwe 
akuyambitsa (Njira ya) kulenga 
(zolengedwa), Kenako 
adzakubwezanso (kulengako 
Pambuyo pa imfa yawo), kenako 
Mudzabwezedwa kwa lye (kuti 
Mudzaweruzid we) . 

12. Ndipo tsiku limene nthawi 
ya chiweruzo (Kiyama) 
idzakwana, oipa adzataya Mtima 
(zakupeza mtendere wa Mulungu). 

13. Ndipo sadzakhala ndi 
aomboli ochokera M'mafano awo, 
ndipo mafano awowo 
Adzawakana. 












'*$£&&&*&> 
*&,#*$&$&'&« 



Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



857 



n *>i 



r • f jjji oj^ 



14. Ndipo tsiku limene nthawi 
ya chiweruzo (Kiyama) 
idzakwana, tsiku limenelo 
Adzalekana (ena kukalowa 
kumunda Wamtendere, pomwe ena 
akalowa Kumoto). 

15. Koma amene akhulupirira 
ndi Kumachita zabwino, adzakhala 
M'minda ya zipatso ndi maluwa 
Akusangalatsidwa. 

16. Ndipo amene 
sadakhulupirire ndi Kutsutsa aya 
Zathu ndi za kukumana ndi tsiku 
Lomaliza, iwo adzaperekedwa ku 
Chilango cha moto. 

17. Choncho, lemekezani 
Mulungu pamene Mukulowa 
m' nthawi za usiku (Popemphera 
Magaribi ndi Isha); ndi Pamene 
mukulowa m' nthawi ya 
M'bandakucha (popemphera 
Pemphero la Fajiri). 

18. Kutamandidwa konse, 
kumwamba ndi Pansi nkwa 
Mulungu. Ndipo (Mulemekezeni) 
m' nthawi ya madzulo 
(Popemphera Aswiri) Ndi pomwe 
mukulowa M' nthawi yamasana 
(Zuhuri). 

19. (lye) amatulutsa chamoyo 
kuchokera Mchakufa, ndipo 
amatulutsa chakufa Kuchokera 
m' chamoyo, ndipo Amaukitsa 
nthaka pambuyo pachilala Chake. 















o 1 












<j&% ^aiUii (io^ii 4$i 






Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



858 



Y> *>i 



r • fJj* 1 *J>" 



Ndipo momwemonso 
Mudzatulutsidwa (m'manda). 

20. Ndipo zina mwazizindikiro 
Zake (zosonyeza Mphamvu Zake 
zoposa), ndiko Kukulengani 
kuchokera ku dothi kenako Inu 
nkukhala anthu omwe mukufala 
(Ponseponse). 

21. Ndipo zina mwazizindikiro 
Zake (Zosonyeza chifundo Chake 
kwa inu) Ndiko kukulengerani 
akazi a mtundu wanu Kuti 
mukhazikike (mitima yanu) Kwa 
iwo, ndipo adaika Pakati panu 
chikondi ndi chisoni. Ndithu, 
mzimenezi muli zizindikiro Kwa 
anthu amene amalingalira. 

22. Ndipo zina mwazizindikiro 
Zake (Zosonyeza kukhoza Kwake) 
ndiko Kulenga kwa thambo ndi 
nthaka Ndikusiyana kwa 
ziyankhulo zanu ndi Utoto (wa 
makungu anu; chikhalirecho 
Mudalengedwa kuchokera kwa 
Munthu m'modzi). Ndithu, 
m'zimenezi Muli zizindikiro kwa 
odziwa. 

23. Ndipo zina mwa zizindikiro 
Zake (Zosonyeza luntha Lake), 
ndiko Kukupatsani mpumulo 
watulo usiku, Ndi (kudzuka) usana 
ndi kufunafuna Kwanu zabwino 
Zake. Ndithu, M'zimenezo muli 
zisonyezo kwa Anthu amene 















Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



859 11 *>< 



r • f jjii 5j>- 



amamva (Ndi kuthandizidwa 
ndikumvako). 

24. Ndipo zina mwazizindikiro 
Zake (Zosonyeza mphamvu Zake 
zoposa) Ndiko kukusonyezani 
kung'anima Komwe 
kumakuchititsani mantha, Ndi 
kukupatsani chiyembekezero 
(Chakudza kwa mvula). Ndipo 
Amatsitsa madzi kuchokera 
kumwamba. Kotero kuti amaukitsa 
nthaka ndi Madziwo pambuyo pa 
chilala chake (Nthakayo). Ndithu, 
m'zimenezi Muli zizindikiro kwa 
anthu ozindikira. 

25. Ndipo zina mwazizindikiro 
Zake (Zosonyeza kukhoza 
Kwake), ndiko Kuti thambo ndi 
nthaka zaima mwa Lamulo Lake. 
Kenako akadzakuitanani; Kuitana 
kamodzi nthawi imeneyo inu 
Mudzatuluka m' nthaka. 

26. Ndipo onse akumwamba ndi 
a padziko Lapansi, Ngake. Onse 
amamvera lye. 

27. Ndipo lye ndiamene 
adayambitsa Zolengedwa. Ndipo 
ndi Yemwe Adzazibwerezenso 
(kachiwiri). Ndipo 
Kuzibwerezako, nkosavuta kwa 
lye ndipo, AH ndi mbiri yabwino 
Kumwmba ndi pansi.Ndiponso lye 
Ngwamphamvu zoposa 
Ngwanzeru zakuya. 









V>"'i -<1 



"•*"< 9 '• ,»"i.'"V1ii£ "" > . i\ ' 9 ' 



Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



860 



n frji-i 



r • f jjj» Sjj-- 



28. Akuponyerani fanizo la 
chikhalidwe Chanu. Kodi 
(akapolo) amene manja Anu 
akumanja apeza ali ndi gawo 
Pachuma chimene takupatsani 
kotero Kuti mumagawana 
chimenecho Molingana? Kodi 
mumawaopa monga Momwe 
muoperana wina ndi mzake? 
(Nanga nchotani inu kuti 
mumuyese Mulungu kuti ali ndi 
amzake Mwa akapolo Ake?) Umo 
ndimomwe Tikulongosolera aya 
(ndime Zathu) Kwa anthu 
ozindikira. 

29. Koma amene adadzichitira 
zoipa okha, Atsata zofuna zawo 
popanda kudziwa. Kodi ndiyani 
angamulungamitse amene 
Mulungu wamsiya kuti asokere 
(Chifukwa chakusafuna kwake 
Kuongoka?) Ndipo iwo sadzakhala 
ndi Apulumutsi. 

30. Lunjika nkhope yako 
kuchipembedzo Moyenera; (pewa 
kusokera kwa okana Mulungu. 
Dzikakamize ku) chilengedwe 
Chimene Mulungu adalengera 
anthu. (Ichi nchipembedzo cha 
Chisilamu Chomwe nchoyenerana 
ndi chilengedwe Cha 
munthu).Palibe kusintha 

M' chilengedwe cha zolengedwa za 
Mulungu. Ichi ndi chipembedzo 
choona (Cholungama). Koma 
anthu ambiri sadziwa. 



" 

<_>>» 






®h£$i4-&. 



»< >>'\'*'i 









Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 861 * > *>» 



r . ?jj\ oj^ 



31. (Lunjikani nkhope zanu) 
modzichepetsa Kwa lye ndipo 
muopeni (Potsatira malamulo 
Ake). Pempherani Swala, ndipo 
musakhale mwa opembedza 
Mafano (Amushirikina), 

32. Mwa omwe agawa 
chipembedzo Chawo nkukhala 
mipatukomipatuko; Gulu lililonse 
likusangalalira chomwe Lili nacho. 

33. Ndipo mavuto akawakhuza 
anthu, Amampempha Mbuye 
wawo Modzichepetsa kwa lye. 
Kenako Akawalawitsa mtendere 
wochokera Kwa lye, pamenepo 
ena a iwo Amamuphatikiza Mbuye 
wawo (Ndi mafano). 

34. Posathokoza zimene 
tawapatsa. Choncho Sangalalani 
(ndi zimene mukuzifunazo); 
Posachedwapa Mudziwa (kuipa 
kwake). 

35. Kodi kapena tidawatsitsira 
umboni Womwe ukufotokoza 
zomwe adali Kumuphatikiza nazo 
lye (Mulungu). 

36. Ndipo anthu tikawalawitsa 
mtendere, Amausangalalira. Koma 
choipa Chikawapeza, chifukwa cha 
zomwe manja Awo atsogoza, 
pamenepo iwo amataya mtima 
(Kuti sangapezenso zabwino za 
Mulungu). 



i 9 *~\' f'Z&l' 9< { S9 9 9 









il&KiSa&wqS^ 






Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



862 



Y^ j.j*-i 



r • f jjii oj>^ 



37. Kodi saona kuti Mulungu 
Amamchulukitsira riziki yemwe 
Wamfuna, ndi kumchepetsera 
(Yemwe wamfuna.) Ndithu 
m'zimenezi, muli zisonyezo Kwa 
anthu okhulupirira. 

38. Choncho mpatseni gawo 
lake wachibale, M'mphawi ndi 
wapaulendo (Amene alibe 
chokamfikitsa kwawo). Zimenezo 
nzabwino kwa amene Akufuna 
chiyanjo cha Mulungu, Ndipo iwo 
ndiwo opambana. 

39. Ndipo chuma chimene 
mukupatsana M'njira yamphatso 
kuti Chichuluke m'chuma cha 
anthu, kwa Mulungu sichichuluka. 
Koma (chuma) Chimene 
muchipereka m'njira ya Zakati uku 
mukufuna chiyanjo cha Mulungu 
(chimachuluka). I wo wo ndi 
Amene adzapeza mphoto 
yochuluka. 

40. Mulungu ndi Yemwe 
adakulengani. Kenako 
adakupatsani (zokuthandizani Kuti 
mukhale ndi moyo). Kenako 
Adzakupatsani imfa (kuti mulowe 
M'manda). Ndipo kenako 
Adzakuukitsani (kuti 
mukaweruzidwe Pazomwe 
mumachita). Kodi mwa Amene 
mukuwaphatikiza ndi Mulungu, 
Alipo yemwe angachite 
chilichonse M'zimenezi? Wayera 















Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



863 



n *>i 



r ♦ ?jj\ 5j^ 



lye (Mulungu) ndipo Watukuka ku 
zimene akumphatikiza. 

41. Chisokonezo chaonekera 
pamtunda Ndi panyanja chifukwa 
cha zimene Manja a anthu achita, 
kuti awalawitse (Chilango cha) 
zina zomwe adachita; Kuti iwo 
atembenukira (kwa Mulungu). 

42. Nena: "Yendani padziko ndi 
kuyang'ana Momwe adalili 
mathero a omwe adalipo Kale. 
Ambiri a iwo adali ophatikiza 
Mulungu ndi mafano." 

43. Lungamitsa nkhope yako ku 
chipembedzo Choona lisanadze 
tsiku losabwezedwa Lochokera 
kwa Mulungu. Tsiku limenelo 
(Anthu) adzagawikana, (abwino 
Akalowa kumunda wamtendere, 
pomwe Oipa akalowa kumoto). 

44. Amene sanakhulupirire, 
kuipa kwa Kusakhulupirira kwake 
kuli pa iye (Mwini). Ndipo amene 
achita zabwino Iwo akudzikonzera 
okha (zabwino) 

45. Kuti awalipire zabwino 
Zake amene Akhulupirira ndi 
kuchita zabwino. Ndithu, Iye 
sakonda akafiri. (Osakhulupirira). 

46. Ndipo zina mwazisonyezo 
Zake (Zosonyeza mphamvu Zake 
ndi chifundo Chake). Ndiko 
kutumiza mphepo yodza ndi 






^99 9' 9>< 















Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



864 



Y1 tj*r\ 



r • fjj\ ojj^ 



nkhani Yabwino (yakuti mvula 
ivumbwa) ndi kuti Akulawitseni 
chifundo Chake, ndi kuti Zombo 
ziyende (panyanja) mwa lamulo 
Lake, ndi kuti mufunefune 
zabwino Zake ndi Kutinso 
muthokoze (mtendere Wake 
Pomumvera ndi kumpembedza lye 
Yekha). 

47. Ndipo, ndithu tidatuma 
aneneri kwa Anthu awo patsogolo 
pako. Choncho (Mneneri aliyense) 
adawadzera anthu Ake ndi 
maumboni oonekera poyera, 
(Osonyeza kuona kwawo. Koma 
adawakana). Ndipo 
tidawawononga amene adalakwa. 
Ndikofunika kwa Ife kupulumutsa 
Okhulupirira. 

48. Mulungu ndiyemwe 
akutumiza mphepo Yomwe 
imagwedeza mitambo 
mwamphamvu, Ndipo 
akuibalalitsa kumwamba mmene 
Akufunira. Amaigawa 
zigawozigawo (Kufikira) uyiona 
mvula ikutuluka mkati mwake 
(Mitamboyo). Ndipo (Mulungu) 
akaitsitsa kwa Amene wamfuna 
mwa akapolo Ake, pamenepo Iwo 
amakondwa ndi kusangalala. 

49. Ngakhale kuti 
isadawatsikire, Adali otaya mtima 
ndi Kutekeseka kwambiri. 















Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



865 



tl *>» 



r • fjj\ ijj~> 



50. Choncho, yang'ana 
(molingalira) zizindikiro Za 
chifundo cha Mulungu momwe 
Akuukitsira nthaka (pomeretsa 
mmera) Pambuyo pachilala chake. 
Ndithu, lye ndi Yemwe Akuukitsa 
akufa. Ndipo lye Ngokhoza 
Chilichonse (palibe chokanika kwa 
lye.) 

51. Ndipo, ndithu, tikatumizira 
mphepo (Yoononga mmera) 
nkuuona pambuyo pake Uli 
wachikasu, akadakhala akupitiriza 
Kukana Mulungu (chifukwa 
chokwiyitsidwa Ndi zimenezi.) 

52. (Usadandaule ndi makani 
awo). Ndithu, I we sungachititse 
kuti amve akufa (Kuitana kwako). 
Ndiponso sungachititse Kuti amve 
agonthi kuitana pamene 
Akutembenukira nakuyang'anitsa 
Msana (osafuna kumva mawu ako). 

53. Ndipo iwe sungathe 
kuwaongolera akhungu 
M'kusokera kwawo. Sungachititse 
kuti Amve koma okhawo amene 
akhulupirira Aya Zathu. Iwowo 
ndiwo Odzipereka. 

54. Mulungu ndi Yemwe 
adakulengani Kuchokera kudontho 
lofooka; kenako Adakupatsani 
mphamvu pambuyo Pakufooka, 
ndipo pambuyo pamphamvu 
Adakupatsani kufooka ndi imvi, 















*<^S;J-S£ua#*tf 



V 






Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



866 n &\ 



r • ^j\ oj>-» 



(lye) Akulenga chimene wafuna. 
Ndipo lye Ngodziwa kwambiri; 
Ngokhoza Chilichonse. 1 

55. Ndipo tsiku limene 
chiweruziro (Kiyama) 
chidzachitika, oipa adzakhala 
Akulumbira (kuti) sadakhale 
(padziko Lapansi) koma ola 
limodzi. Umo Ndimomwe 
amatembenuzidwira (Kuchokera 
kunjira ya choonadi). 

56. Ndipo amene apatsidwa 
nzeru ndi Chikhulupiriro, 
adzanena: "Ndithu, Inu mudakhala 
m'chilamulo cha Mulungu kufikira 
tsiku louka ku imfa; Tsono ili ndi 
tsiku louka ku imfa koma Inu 
simunali kudziwa". 

57. Tsiku limenelo, madandaulo 
a omwe Adzichitira chinyengo 
sadzawathandiza Ndipo 
sadzafunsidwa kuti 
Amukondweretse Mulungu (ndi 
kulapa Kwawo.) 

58. Ndipo ndithu, tawaponyera 
anthu mafanizo A mtundu 
uliwonse m'Qur'an iyi. Ndipo, 















1 M'ndime iyi akufotokoza kuti adalenga anthu kuchokera m'madzi ofooka. 
Ndipo kuchokera pamenepo chilengedwe chimasinthasintha pokhala khanda, 
mnyamata kenako nkukhala wamkulu wanyongazake ndipo mapeto ake 
nkukhala nkhalamba ya imvi, yofooka. Zonsezi zimachitika mwa chifuniro cha 
Mulungu popanda munthu kuikapo dzanja. 

2 . Ndime iyi ikufotokozera kuti anthu ochita zoipa akadzaukitsidwa m'manda 
ndi kuona zoopsa zothetsa nzeru, adzaganiza kuti pamoyo wa padziko 
lapansi sadakhale nthawi yaitali koma ola limodzi basi. Izi nchifukwa 
chamavuto omwe adzakumana nawo patsiku limenelo. 



Surat 30. Ar-Rum Juzu 21 



867 n *&\ 



r • fjj\ 5j>-» 



ndithu, ukawabweretsera Mtsutso 
uliwonse, anena omwe 
Sadakhulupirire: "Inu sikanthu, 
koma Ndinu anthu ochita 
zachabe". 

59. Mmenemo ndi momwe 
Mulungu Akudindira (chidindo) 
m'mitima mwa Amene sazindikira. 

60. Choncho pirira (iwe 
Mtumiki Kumasautso awo). 
Ndithu, lonjezo La Mulungu, 
nloona, ndipo asakugwetse 
Mphwayi amene alibe 
chikhulupiriro Chotsimikiza 
(Mulungu ndi Mtumiki Wake). 



e <^^i<aK$a* 






&*&&}&&&&&& 



®&&$u$\ 




Siirat 31. Luqman Juzu 21 



868 



n *jh\ 



T ) OUiJ Ojj~t 




Surayi yayamba ndi kufotokoza za Buku la Qur'an ndi zomwe 
zili m'kati mwake monga chiongoko ndi chiflindo. Ndipo 
ikufotokozanso chikhalidwe cha ochita zabwino, pomvera Chauta 
ndi kukhulupirira tsiku lachimaliziro, ndi kutsimikizira kuti 
kupambana kuli pa iwo. 

Pankhaniyi yatsatizapo kufotokoza zakusokera kwa odzikuza ndi 
kupereka mitsutso ndi zisonyezo kwa otsutsa, zosonyeza umodzi wa 
Mulungu; Mleri wa zolengedwa monga kalengedwe kodabwitsa 
kazam'dziko monga thambo, dzuwa, mwezi, nyenyezi, nthaka, 
mapiri, nyanja, mitsinje ndi mmera, ndi zonse zimene munthu 
akuziona zosonyeza luso la Mulungu ndi mphamvu Zake zoposa. 

Surayi yamaliza ndi kuchenjeza anthu za tsiku loopsa lomwe 
munthu sadzathandizidwa ndi ana ake kapena chuma chake. 




Surat31. Luqman Juzu21 



869 



n *>i 



V S OUii 5jj-j 



Surat Luqman XXXI 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Alif-Lam-Mirn. 

2. Izi ndi aya za Buku 
Lokonzedwa bwino. 

3. (Lomwe ndi) chiongoko ndi 
chifundo Kwa ochita zabwino, 

4. Amene akupemphera swala 
ndi Kupereka chopereka (zakati) 
omwenso Akutsimikiza za tsiku 
lachimaliziro. 

5. Iwowo ali pa chiongoko 
chochokera Kwa Mbuye wawo; 
ndipo iwowo Ndiwo opambana. 

6. Koma alipo ena mwa anthu 
amene Akusankha nkhani ya bodza 
(Ndi kumaifotokoza kwa anthu) 
Ndi cholinga choti awasokeretse 
ku Njira ya Mulungu. Popanda 
kuzindikira. Ndipo akuichitira 
zachipongwe (njira ya Mulunguyi) 
Iwo adzapeza chilango 
chowasambula. 






^c^T^ap 



2;s&mi 



o&g\^3^j 



^ 



©ifi 












Malembo awa akudziwitsa kuti Qur'an idalembedwa mwachidule chomveka 
ndi kulozera kuti Bukuli lomwe ilo anthu anzeru zakuya akulephera kulemba, 
lapangika kuchokera m'malembo amenewa omwe anthu akuwadziwa ndi 
kugwiritsa ntchito. Ngati iwo ali ndi chipeneko kuti silidachokere kwa Mulungu, 
koma kuti Muhammad (SAW) adangolilemba yekha ngakhale kuti adali 
wosadziwa kulemba, atalemba Buku lawo longa ili. Malembo a Bukuli ndi 
omwenso iwo amawadziwa. Komatu sangathe kulemba Buku longa ili 
ngakhale anthu onse am'dziko lapansi atathandizana. Uwu ndi umboni 
waukulu umene ukusonyeza kuti Bukuli lidachokera kwa Mulungu. 



Siirat31. Luqman Juzu 21 



870 



n *>i 



V \ OUii 5jj-» 



7. Ndipo pamene aya Zathu 
Zilakatulidwa kwa iye, 
Akuzitembenuzira msana 
modzikuza Ngati kuti sanazimve, 
ngati kutinso M'makutu mwake 
muli ugonthi Choncho muuze 
nkhani ya chilango Chopweteka. 

8. Ndithu, amene akhulupirira 
ndi kumachita Zabwino, adzakhala 
ndi minda Yamtendere. 

9. Adzakhala m'menemo muyaya. 
Hi Nlonjezo la Mulungu lomwe lili 
loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu; 
Ngwanzeru Zakuya. 

10. Adalenga thambo popanda 
mizati Yomwe mukuiona. Ndipo 
adaika mapiri M'nthaka kuti 
isakugwedezeni. Ndipo (Iye) 
adafalitsa nyama M'menemo 
zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo 
tidatsitsa madzi kuchokera ku 
Mitambo, choncho tidameretsa 
m'menemo (M'nthaka)mmera 
wokongola wamitundu 
Yosiyanasiyana. ] 

11. Izi (zonse) nzolengedwa za 
Mulungu. Choncho,tandisonyezani, 
nchiyani Adalenga amene sali 









,»»<*fi 



©, 









M'ndime iyi Mulungu akutifotokozera kuti adalenga thambo monga lilili 
m'kukula kwake ndi m'kuphanuka kwake ndi kulimba kwake popanda mizati 
yolichirikiza. Ndipo inu anthu mukuliona mmene lili lopanda chilichonse 
choligwira koma mphamvu za Mulungu Wamkulu Wapamwambamwamba. 
Ndipo m'nthaka adaikamo mapiri akuluakulu kuti nthaka isamagwedezeke ndi 
kumakusowetsani mtendere, kapena kumakugumulirani nyumba zanu. Ndipo 
Mulungu adafalitsa padziko zamoyo zochuluka ndi kumeretsa mbewu 
zosiyanasiyana. Zonsezi zikusonyeza mphamvu Zake zoopsa. 



Surat31. Luqman Juzu 21 



871 



y\ frjA-i 



t ^ ouiJ ojj^t 



Mulungu. Koma Odzichitira okha 
zoipa ali Mkusokera koonekera. 

12. Ndipo ndithu, tidampatsa 
Luqman Nzeru (ndipo tidati kwa 
iye): "Thokoza Mulungu (pazimene 
Wakupatsa)." Ndipo, amene 
athokoza, Ndithu kuthokozako 
Kumthandiza yekha, ndiponso amene 
Akana (mtendere wa Mulungu 
Pakusiya kuthokoza), ndithu, 
Mulungu Ngwachikwanekwane 
Ngotamandidwa 

13. Ndipo (akumbutse) pamene 
Luqman Adauza mwana wake 
akumulangiza: "E, iwe mwana 
wanga! Usaphatikize Mulungu ndi 
mafano. Ndithu, Kumuphatikiza 
(Mulungu), ndi Kuipitsa 
kwakukulu." 

14. Ndipo tamulangiza munthu 
kwa makolo Ake (kuwachitira 
zabwino) adamsenza (Pathupi) mai 
wake ali wofooka Pamwamba 
pakufooka. (Adamuyamwitsa) Ndi 
kumusiyitsa patapita zaka ziwiri. 
Ndithokoze Ine ndi makolo ako, 
Kwa Ine nkobwerera. 












©. 



99 "\ i '< i V 



1 M'ndime izi 13 mpaka 14 Mulungu akulamula munthu kuti achitire zabwino 
makolo ake powamvera ndi kuwathandiza ngati ali osowa. Izi nchifukwa cha 
kuti makolo ake adazunzika kwambiri pomulera iye makamaka mayi wake ndi 
amene adazunzika kwambiri kuyambira pamene adatenga mimba yake 
kufikira pamene adamusiyitsa kuyamwa. Choncho mverani makolo anu 
pazimene akukulangizani zomwe sizili zolakwira Mulungu. Koma ngati 
akukulangizani zolakwira Mulungu, musatsatire malangizo awowo, koma 
khalani nawoni mwa ubwino. 



Surat31. Luqman Juzu21 872 m^ ^ l 



t\ ouii ojj-- 



15. Ndipo (makolo ako) ngati 
Atakukakamiza kuti undiphatikize 
Ine Ndi zomwe iwe sukuzidziwa, 
Usawamvere; koma khala nawo 
Padziko mwaubwino; ndipo tsatira 
njira Ya amene atembenukira kwa 
Ine. Ndipo Kenako kobwerera 
kwanu nkwa Ine. Choncho 
ndidzakuuzani zimene Mudali 
kuchita. 

16. "E, iwe mwana wanga! 
Ndithu, (Chabwino ndi choipa cha 
munthu) icho Ngakhale chitakhala 
cholemera ngati Njere za mpiru 
ndi kukhala m'kati Mwa thanthwe 
kapena m'kati mwa Thambo, 
kapena m'kati mwa nthaka, 
Mulungu adzachibweretsa (ndi 
Kumulipira amene adachita). 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa zinthu 
zobisika, (Ndiponso) Ngodziwa 
zinthu zoonekera. 

17. E, iwe mwana wanga! 
Pemphera moyenera, Lamula 
zabwino, letsa zoipa, ndipo Pirira 
ndi masautso amene akukhudza. 
Ndithu zimenezo ndizinthu zofunika 
Kuziikirapo mtima (munthu aliyense) 

18. Ndipo usatembenuze tsaya 
lako kwa anthu (Modzikweza,) 
ndipo usayende padziko Monyada. 
Ndithu, Mulungu sakonda Yense 
wodzitukumula, wonyada. 

19. Ndipo lingana m'kuyenda 
kwako (Popanda kufulumiza 





















Surat 31. Luqman Juzu 21 I 873 I T ^ *jJt-i 



x \ juii 5jj-* 



kwambiri Kapena kuyenda 
pang'onopang'ono); Ndipo tsitsa 
mawu ako (Ukamayankhula), 
chifukwa, mawu Okweza ngoipa 
kwabasi). Ndithu mawu Oyipitsitsa 
ndi mawu a bulu." 

20. Kodi simuona kuti Mulungu 
Adakugonjetserani zakumwamba 
Ndi zapansi ndi kukukwaniritsirani 
Chisomo Chake, chobisika ndi 
Choonekera? Ndipo alipo ena mwa 
Anthu amene akukangana Pa za 
Mulungu popanda kuzindikira 
Ngakhale chiongoko, ngakhalenso 
BukuLounika. 1 

21. Ndipo akauzidwa kuti: 
"Tsatani zimene Mulungu 
watsitsa," akunena: "Koma 
Tikutsata zimene tidawapeza nazo 
Makolo athu." Kodi ngakhale kuti 
Satana akuwaitanira ku chilango 
Chamoto (woyaka, adzatsatirabe)? 

22. Ndipo amene akupereka 
nkhope yake Kwa Mulungu 
(amene akugonjera Mulungu 
kwatunthu) ali ochita Zabwino, 
ndiye kuti wagwira Chogwirira 
cholimba. Ndipo mapeto A zinthu 
zonse nkwa Mulungu basi. 



^&39£ft#& 












1 E, inu anthu! Ndithu, Mulungu Wolemekezeka adakupangirani zonse zili 
kumwamba monga dzuwa mwezi, nyenyezi kuti muthandizike nazo. Ndipo 
adakupangirani zonse zomwe zili m'nthaka monga mapiri, mitengo, zipatso, 
mitsinje, ndi zina zambiri zosawerengeka kuti zonsezi zigonjere inu ndikuti 
muthandizike nazo 



Surat31. Luqman Juzu 21 



874 



tl ij*r\ 



t ^ ou£J ojj*> 



23. Koma amene 
sadakhulupirire (Mulungu ndi 
Mtima wake wonse) choncho 
Kusakudandaulitsekusakhulupirira 
kwake. Kobwerera kwawo nkwa 
Ife basi. Kumeneko Tidzawauza 
zimene adachita. Ndithu, Mulungu 
Ngodziwa zonse zam'zifuwa. 

24. Tikuwasangalatsa pang'ono 
(apo Padziko lapansi). Kenako 
Tidzawakankhira kuchilango 
chokhwima. 

25. Ndipo ukawafunsa: "Ndani 
adalenga thambo Ndi nthaka?" 
Ndithu anena: "Ndi Mulungu." 
Nena: "Kutamandidwa Konse 
nkwa Mulungu." Koma ambiri a 
iwo sadziwa. 

26. Zonse zakumwamba ndi za 
pansi, nza Mulungu. Ndithu, 
Mulungu Ngwachikwanekwane, 
Ngotamandidwa. 

27. Ndipo ndithu, ngakhale 
mitengo yonse Hi m'nthaka 
ikadakhala zolembera, Ndipo 
nyanja (nkukhala inki), 
Ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi 
Nyanja zisanu ndi ziwiri, Mawu a 
Mulungu sakadatha. Ndithu, 
Mulungu Ngwamphamvu, 
Wanzeru zakuya. 



1 Ndime iyi ikufotokoza kuti Mawu a Mulungu ngochuluka. Mitengo yonse 
padziko lapansi itakhala ngati mapensulo ndipo nyanja zonse padziko lapansi, 
nkuwonjezanso nyanja zina, zikadakhala inki, zonse zikadatha koma Mawu a 
Mulungu alipobe. 






® 



Surat 31. Luqman Juzu 21 875 Y > i£-\ 



T ) JUaJ tjj~* 



28. Kulengedwa kwanu, 
ngakhale Kuukitsidwa kwanu 
m'manda sikuli Kanthu koma kuli 
ngati (kulenga Kapena kuukitsa 
kwa) munthu Mmodzi.(Palibe 
chokanika kwa Mulungu).Ndithu, 
Mulungu Ngwakumva Ngopenya 
chilichonse. 

29. Kodi suona (kuona 
kolingalira) kuti Mulungu 
amalowetsa nthawi ya usiku 
Muusana, ndipo amalowetsa 
nthawi Ya usana muusiku; ndipo 
adagonjetsa Dzuwa ndi mwezi. 
Chilichonse Chikuyenda 
mwanthawi imene Idaikidwa? 
Ndithu Mulungu akudziwa Zonse 
zimene mukuchita. 

30. Izi nchifukwa chakuti 
Mulungu, lye Ngoona; ndipo 
zomwe akuzipembedza Kusiya 
lye, nzonama. Ndipo ndithu, 
Mulungu ndiye Wotukuka Wamkulu. 

31. Kodi suona kuti zombo 
zikuyenda Panyanja mwamtendere 
wa Mulungu Kuti akusonyezeni 
zisonyezo (Zamtendere Wake)? 
Ndithu M'zimenezo muli 
zisonyezo kwa yense Wopirira, 
wothokoza. 

32. Ndipo mafunde onga 
thambo Akawavindikira, 
amampempha Mulungu 
Modzipereka kwambiri. Koma 



m^^%m%'M^c 



<?9 "<{ 9 9 '*\ . 












Surat31. Luqman Juzu21 



876 



n *>i 



V > OUiJ Sjj-* 



Akawapulumutsira kumtunda, ena 
A iwo amachita zolungama. 
(Koma Ena a iwo amakana 
mtendere wa Mulungu). 
Sangawakane mau Wathu Koma 
yense wachinyengo wosathokoza. 

33. E, inu anthu! Muopeni 
Mbuye wanu (Potsatira malamulo 
Ake ndi kusiya Zoletsedwa); ndipo 
liopeni tsiku Limene tate 
sadzathandiza mwana Wake, 
ngakhalenso mwana Sadzathandiza 
tate wake chilichonse.Ndithu, 
lonjezo la Mulungu nloona; 
Usakunyengeni moyo wadziko 
lapansi, Ndiponso asakunyengeni 
Mdyerekezi pa za Mulungu, 

34. Ndithu, kudziwa kwa 
nthawi (yakutha Kwa dziko) kuli 
ndi Mulungu (yekha). lye 
ndiamene amavumbwitsa mvula 
(Nthawi imene wafuna); ndipo 
Akudziwa zimene zili 
m'ziberekero (Mwa zolengedwa 
zake:zachimuna Kapena 
zachikazi). Ndipo aliyense sadziwa 
Chomwe apeze mawa; (chabwino 
kapena Choipa); ndiponso 
sadziwa aliyense Kuti ndi dziko liti 
adzafera. Ndithu, Mulungu 
ngodziwa ndiponso Wodzindikira 
Mmene zinthu zilili. 












Surat32. As-Sajdah Juzu21 



877 



T \ ij}r\ VY o*b^-Jl Ojj-j 




SURAT AS-SAJDAH XXXII 




Surayi idavumbulutsidwa pambuyo pa Sura ya Muuminina. 
Ndipo ikufotokoza za kutsika kwa Qur'an ndi udindo wa 
Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye); 
kalengedwe ka thambo ndi nthaka; kalengedwe ka munthu 
komwe nkosinthasintha; zoyankhula za otsutsa, kuuka ku imfa 
ndi kuwayankha mtsutso ndi zizindikiro za chilengedwe zimene 
zikusonyeza mphamvu za Mulungu zoposa, Amene sangalephere 
kuukitsa anthu ku imfa. 

Nkhani yaikulu m' Surayi ndikudzutsa anthu kuti apenye 
zizindikiro za chilengedwe zimene zikusonyeza mphamvu za 
Mulungu zoposa, Amene sangalephere kuukitsa anthu ku imfa. 




Surat 32. As-Sajdah Juzu 21 878 t \ *>» r t 5u*~Ji a^ 



SuratAs-Sajdah XXXII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1 . yi lif-Ldm-Mim. 

2. Chivumbulutso cha Buku (la 
Qur'an) Chilibe chikaiko mkati 
mwake chochokera Kwa Mbuye 
wa zolengedwa. 

3. Kodi (Akuraishi 
osakhulupirira), akuti: "Walipeka 
yekha (ndi kumnamizira 
Mulungu)?" Iyayi, ichi Nchoona 
chimene (chavumbulutsidwa Kwa 
iwe) uchokera kwa Mbuye wako 
Kuti uwachenjeze anthu 
ndichimenechi, Amene 
sadawadzere mchenjezi Iwe 
usadadze.Kuti aongoke (ndi 
Kutsatira njira yolungama). 

4. Mulungu ndi Yemwe 
adalenga thambo Ndi nthaka ndi 
zapakati pake M'masiku asanu ndi 
limodzi; ndipo Adakhazikika pa 
mpando Wake Wachifumu; 
(kukhazikika kolingana Ndi 
ulemerero Wake, kumene lye 
Mwini wake akukudziwa). Inu 
mulibe Mtetezi ngakhale 
muomboli kupatula lye. Nanga 
kodi bwanji simulingalira? 1 






o^)t<^j)^U- 



-^ 



" 99' 9' 9)4'\ luV "* ^ 






1 .M'ndime iyi Mulungu akutiuza kuti adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati 
pake m'masiku asanu ndi limodzi. Komatu nthawi ya masiku amenewa, palibe 



Surat32. As-Sajdah Juzu 21 



879 



t ^ frjA-i vy ojbtc^Ji djj-- 



5. (lye) akuyendetsa zinthu 
(zonse) kumwamba Ndi pansi. 
Ndipo kenako mapeto ake, (zonse) 
Zimakwera kubwerera kwa lye, pa 
tsiku Lolingana ndi zaka chikwi 
chimodzi (Poyerekeza ndi zaka 
zadziko lapansi)Zomwe inu 
mumawerengera. 

6. Ameneyo, ndi Mulungu 
(Mwini kulenga ndi Kuyendetsa 
zinthu), Wodziwa zobisika ndi 
zoonekera; Mwini mphamvu 
zoposa Wachisoni, 

7. Yemwe adakonza bwino 
chilengedwe Cha chilichonse. 
Ndipo adayambitsa Chilengedwe 
cha munthu kuchokera Kudongo. 

8. Kenako adachita mbumba 
yake kuti Ipangike kuchokera 
m'madzi enieni Opandapake. 

9. (Ndipo) kenako adamkonza 
Ndi kumuuzira Mzimu Wake. 
Ndipo adakulengerani Makutu, 
maso ndi moyo. Kuthokoza 
Kwanu mpang'ono ndithu, 

10. Ndipo (otsutsa kuuka ku 
imfa) akunena: "Kodi 
tikadzatayika m'nthaka (ndi 
Kusakanikirana ndi dothi), 
Tidzalengedwanso mwatsopano?" 
(Iyayi),Koma iwo sakhulupirira, za 
kukumana Ndi Mbuye wawo. 






^-vJ$£s$&*^ 



3±\zy&t£$^&& 



,-V \J* ^ "'"-^ 






^J3J^> J H^ 



amene akudziwa tsatanetsatane wake koma Mulungu yekha. Choncho 
tisaganizire kuti masikuwo adali olingana ndi masiku amoyo uno wadziko lapansi. 



Surat 32. As-Sajdah Juzu 21 



880 



n *>i 



rt dj^^Ji 5j_^» 



11. Nena: "Adzachotsa mizimu 
yanu Mngelo Wa imfa, yemwe 
wapatsidwa udindo Umenewu pa 
inu. Kenako Mudzabwezedwa kwa 
Mbuye wanu." 

12. Ndipo ukadawaona oipa 
atazolikitsa mitu Yawo kwa 
Mbuye wawo (uku akunena): "E, 
Mbuye wathu! Taona, ndipo 
tamva. Choncho tibwezeni. 
Tikachita ntchito Zabwino. Ndithu, 
tsopano tatsimikiza 
(Kukhulupirira)." 

13. Ndipo tikadafuna, 
tikadampatsa munthu Aliyense 
chiongoko chake (Momukakamiza 
monga momwe Tidawachitira 
angelo, koma munthu 
Adapatsidwa mphamvu ndi ufulu 
Wozisankhira chimene afuna; 
chabwino Kapena choipa). Koma 
Mawu Atsimikizika ochokera kwa 
Ine: "Ndithu, ndizadzazitsa 
Jahannama Ziwanda ndi anthu; 
onse pamodzi (Amene ali oipa)." 

14. "Choncho, lawani chifukwa 
cha Kusalabadira kwanu 
kukumana ndi Tsiku lanu ili. 
Ifenso tikusiyani (ku Chilango 
monga ngati takuiwalani). Tero 
Lawani chilango chamuyaya, 
Chifukwa cha zomwe munkachita." 

15. Ndithu, amene 
akukhulupirira aya Zathu, 



£8te$*9$&$gX%& 



®6y^y &»M& 












«& 



&&Mm%k&$2i 



\j>>*>& 



Surat32. As-Sajdah Juzu 21 881 ^ *>' rr 5o*-Ji 3 j^ 



ndiamene akuti pamene 
Akulangizidwa ndi ayazo, amagwa 
Kusujudu ndi kulemekeza Mbuye 
Wawo pamodzi ndi kumthokoza. 
Ndipo iwo sadzitukumula. 

16. Nthiti zawo zimalekana ndi 
malo ogona (Usiku), chifukwa 
chopembedza Mbuye Wawo, 
poopa chilango chamoto ndi 
Kulakalaka munda wamtendere. 
Ndipo Amapereka (zakati ndi 
sadaka) M'zimene tawapatsa. 

17. Mzimu uliwonse sudziwa 
zimene Aubisira zotonthoza diso 
(zosangalatsa Moyo ku munda 
wamtendere) monga Mphoto 
pazimene unkachita. 

18. Kodi Msilamu wokwanira 
angafanane Ndi wotuluka 
m'chilamulo cha Mulungu? 
Sangafanane. 

19. Kwa amene akhulupirira ndi 
kumachita Zabwino, adzalandira 
minda Yokhalamo yokongola, 
monga Phwando lawo pazimene 
ankachita. 

20. Koma kwa amene adachita 
zoipa Potuluka m'chilamulo cha 
Mulungu, Malo awo ndi kumoto. 
Nthawi iliyonse Akafuna 
kutulukamo,Azikabwezedwamo 
ndipo Azidzauzidwa: "Lawani 
chilango Chamoto, chomwe 
munkachitsutsa." 



^i^^ij^jl^ 



\V'<i'\ 









®u&\}w$&m 












Surat32. As-Sajdah Juzu21 



882 



V \ frji-l fY o*t*~Jl djj-- 



21. Ndipo ndithudi, tiwalawitsa 
chilango Chocheperapo (padziko 
lapansi) Chisanafike chilango 
chachikulu (cha Tsiku lomaliza), 
kuti atembenuke, (Alape). 

22. Kodi ndani wachinyengo 
kwambiri, Woposa yemwe 
akukumbutsidwa aya Za Mbuye 
wake, kenako nkuzikana? Ndithu, 
Ife, tidzawabwezera zoipa Anthu 
oipa. 

23. Ndipo ndithu, Musa 
tidampatsa Buku . Choncho 
usakhale ndi chikaiko pa 
Zakukumana Naye (Mulungu). 
Ndipo Tidalichita (Bukulo) 
kukhala Chiongoko cha ana a 
Israeli. 

24. Ndipo ena mwa iwo 
tidawachita Kukhala atsogoleri 
oongola (anthu) Mwa lamulo lathu, 
pamene adapirira; Ndipo adali 
kuvomereza motsimikiza Aya Zathu. 

25. Ndithudi Mbuye wako ndi 
Yemwe Adzaweruza pakati pawo 
tsiku Lomalizira pazimene 
amakangana. 

26. Kodi sizidadziwike kwa iwo 
kuti Ndimibadwo ingati imene 
tidaiononga Patsogolo pawo; 
(chikhalirecho iwo) Akudutsa 
mokhala mwawo? Ndithu, 
M'zimenezo, muli 
zizindikiro.Kodi sakumva? 















5J*i^i(!s£i<i&A 









$ 






Surat32. As-Sajdah Juzu 21 I 883 ^ *>' TY sa^-JUjj^ 



27. Kodi sakuona kuti 
timapereka madzi Kunthaka 
youma; ndipo ndi madziwo 
Tikumeretsa mmera umene ziweto 
Zawo zimadya ndi iwo omwe; 
Kodi sakuona? 

28. Ndipo akunena: 
"Kulamulidwa Kumeneku (kwa 
tsiku lachimaliziro) Kudzachitika 
liti, Ngati mukunenadi zoona?" 

29. Nena: "Tsiku 
lachiweruzolo, amene 
Sadakhulupirire, chikhulupiriro 
chawo Sichidzawathandiza. Ndipo 
Sadzapatsidwa nthawi 
yoyembekezera (Kuti mizimu 
yawo isachoke ayambe 
Akhulupirira kaye, mngero wa 
imfa Akadzawadzera?)." 

30. Choncho apatuke; ndipo 
yembekezera (Zimene Mulungu 
wakulonjeza). Ndithu, nawonso 
akuyembekezera (Zimene 
Mulungu wawalonjeza). 












^^ptiSJ&s- <J^^ 



©fci L ' 




Surat33. Al-Ahzab Juzu 21 



884 



t \ *jk-\ rr ^\y*t\ oji- 




Sura ya Ahzab ndiimodzi mwa zimene zidavumbulutsidwa ku 
Madina. Ikufotokoza mbali ina ya malamulo a mbado wa mtundu 
wa Chisilamu, monga momwe zilili sura zovumbulutsidwa ku 
Madina. 

Surayi yafotokoza zamoyo wa Asilamu munthu 
payekhapayekha, ndi pagulu, makamaka pazinthu zapabanja. 
Ndipo yakhazikitsa malamulo odzetsa mtendere ndi chisangalalo 
ku mtundu. Ndipo yathetsa zizolowezi zina zomwe ankachita 
anthu akale, monga mwana wobala wina nkumuyesa ngati wako 
chifukwa chomulera, komanso kumuyesa mkazi wako ngati 
mayi wako. Amakhulupiriranso kuti mwa munthu muli mitima 
iwiri. 

Titha kufotokoza mwachidule mitu ikuluikulu yomwe ili 
m' suramu motere : - 

l)Kuongolera kumiyambo yofunika kuitsata m'Chisilamu 
2)Kufotokoza za Malamulo a Mulungu 
3)Kufotokoza nkhani ya nkhondo ziwiri: ya Ahzab ndi ya 
Ban kuraidhwa 

M'mutu woyambau, mwadza nkhani yofotokoza miyambo 
yokhalirana wina ndi mnzake pagulu, monga miyambo ya 
pachisangalalo cha ukwati, ndi mkazi kudziphimba thupi lonse, 
ndi kuti asayendeyende m'misewu uku atadzikongoletsa ndi 
cholinga choti akaonedwe ndi amuna. Ndi Miyambo 
yokhalirana ndi Mtumiki wa Mulungu, Muhammad (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) ndi kumlemekeza. Ndi miyambo 
yofunika kuitsata pokhalirana pafuko. 

Tsono m'mutu wachiwiri, mwadza nkhani ya malamulo 
oletsa kumuyesa mkazi monga mayi wako, ndi mwana 
womulera chabe monga mwana wako, ndi woyenera kulandira 
chuma chamasiye, ndi chilolezo chokwatira mkazi amene 



Surat33. Al-Ahzab Juzu 21 



885 



y > ij*r\ rr i~>\yH\ «;>-» 



wasiyidwa ndi mwana yemwe udali kumlera chabe, ndi zamitala 
ya Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndi zolinga 
za mitalayo. Ndiponso lamulo lopempherera madalitso Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye,) ndi malamulonso ena 
omwe adakhazikitsidwa. 

Tsono m'mutu wachitatu, Surayi ya fotokoza mwatsatanetsatane 
za nkhondo ya Khandaki yomwe imatchedwanso nkhondo ya 
Ahzab. Ndipo yapereka chithunzi chakuya kwambiri pachimvano 
chamagulu ambiri a anthu pochitira upandu Asilamu. 

Ndipo Surayi yavundukula zachinsinsi cha Amunafikina ndi 
kuchenjeza zakutsatira njira zawo zachinyengo ndi zokaikitsa. 
Ndipo yatalikitsa nkhani yawo kuyambira pachiyambi cha 
Surayi ndi kumalekezero ake kufikira siidawasiyire chobisika 
chilichonse. 

Ndipo yakumbutsa Asilamu za mtendere waukulu wa 
Mulungu powabweza m'mbuyo adani awo popanda chopindula 
adani wo, pamene Mulungu adawalimbikitsa Asilamu ndi angero 
ndi mphepo ya mkuntho imene idaononga katundu wa adani. 

Surayi yafokozanso zankhondo ya Bani Kuraidhwa ndi 
kuswa kwa Ayuda mapangano omwe adalipo pakati pawo ndi 
Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye). 

Surayi ikutchedwa Ahzab chifukwa cha kuti mafuko onse a 
Arabu ndi Ayuda, adasonkhana ndi kumvana kuthira nkhondo 
Asilamu monga dzanja limodzi. 




Surat33. AI-Ahzab Juzu21 



886 



y \ frjA-i rr *->\yH\ *;>- 



Surat AUAhzab XXXIII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. E, iwe Mneneri! Pitiriza 
kuopa Mulungu,ndipo usamvere 
Osakhulupirira ndi achiphamaso. 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa 
kwambiri; Wanzeru zakuya 
(m'zoyankhula Ndi m'zochita 
Zake). 1 

2. Ndipo tsata zimene 
zikuvumbulutsidwa kwa iwe 
kuchokera kwa Mbuye wako 
(Pozigwiritsa ntchito). Ndithu, 
Mulungu Ngodziwa zonse zimene 
mukuchita. 

3. Ndipo yadzamira kwa 
Mulungu; ndipo Mulungu 
akukwana kukhala Msungi ndi 
Mtetezi (wako). 

4. Mulungu sadaike m'chifuwa 
cha Munthu mitima iwiri. Ndipo 
sadachite Akazi anu amene 
mukuwayesa ena Mwa iwo monga 



wm^&m 



^ I 



Q^t^t^U- 



~& 









4$&\$&\&jz 









LSura iyi ikutchedwa Sura ya Ahzab kutanthauza kuti namtindi wa anthu. 
Zimenezi zidali chonchi kuti pamene Chisilamu chimafala mu Mzinda wa 
Madina Munawara momwe mumakhalanso Ayuda, adachita nsanje yaikulu 
Ayudawo. Ndipo akuluakulu awo adaganiza zopita ku Makka kukakopa Arabu 
akumeneko kuti athandizane kuthira nkhondo Asilamu. Choncho Arabu a ku 
Makka adauza mitundu yonse yopembedza mafano kuti akamthire nkhondo 
Muhammad(SAW) ndi kuthetseratu chipembedzo cha Chisilamu. Tero 
adagwirizana ndipo adauzinga Mzinda wa Madina mbali zonse. Koma Mulungu 
adatumiza angero ndi chimphepo chamkuntho chomwe chidamwazamwaza 
katundu wawo. Pachifukwa ichi, onse adathawa. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 21 I 887 I * > *& TT ^>\^H\ &;>- 



amayi anu, kukhala Mayi anu 
enieni. Ndipo Sadachite ana anu 
ongowalera kukhala Ana anu 
enieni (monga inu 
Mukuwatchulira). Zimenezo ndi 
zolankhula Zanu za m'milomo 
mwanu chabe.Koma Mulungu 
akunena choona; lye Akuongolera 
ku njira yoongoka. 

5. Aitaneni ndi maina a atate 
awo. Kutero Ndichilungamo kwa 
Mulungu. Koma Ngati 
simukuwadziwa atate awo, 
(Aitaneni ngati) abale anu 
Pachipembedzo; ndiponso ndi 
anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa 
zimene Mwazichita molakwitsa 
(mosazindikira). Koma (pali 
uchimo) pazimene mitima Yanu 
yachita mwadala. Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka kwabasi, 
Ngwachisoni. 

6. Mneneri ngofunika kwambiri 
kwa Okhulupirira kuposa moyo 
wawo,(Matupi awo ndi chuma 
chawo); ndipo Akazi ake ndi 
amayi awo (amayi a Asilamu; 
nkoletsedwa kuwakwatira 
Pambuyo pa imfa yake). Ndipo 
achibale Pakati pawo ngoyenera 
(kulandira Zamasiye pamalamulo 
a) m'Buku la Mulungu kuposa 
Asilamu ena Ngakhalenso 
Amuhajirina (amene Adasamuka 
ku Makka kupita ku Madina 












Siirat33. Al-Ahzab Juzu 21 



888 



r \ *>» rr v 1 ^ 1 s^ 



chifukwa cha chipembedzo Cha 
Chisilamu). Koma ngati mutachita 
Zabwino kwa anzanu (sikuipa). Izi 
zidalembedwa kale m'buku. 1 

7. Ndipo (akumbutse) pamene 
tidalandira Kuchokera kwa 
Aneneri onse Pangano lawo. Ndi 
kwa iwe, ndi kwa Nuhi, Ibrahim, 
Musa, ndi Isa mwana wa 
Mariyamu. Ndipo tidatenga kwa 
iwo pangano La mphamvu (kuti 
adzafikitsa uthenga Wa Mulungu 
kwa anthu ndi kuitanira Anthu ku 
chipembedzo cha Mulungu). 

8. Kuti (Mulungu) adzafunse 
(Aneneri) oona (Tsiku la 
chimaliziro) pazimene adanena 
(Kwa anthu awo zakufikitsa uthenga 
Woonadi kwa iwo). Ndipo Mulungu 
wawakonzera (Osakhulupirira) 
chilango chopweteka. 

9. E, inu amene 
mwakhulupirira! Kumbukani 
mtendere wa Mulungu Umene uli 
pa inu, pamene adakudzerani Magulu 
ankhondo. Ndipo Tidawatumizira 
mphepo ndi magulu A nkhondo (a 
angero) amene Simudawaone. 
Ndipo Mulungu Akuona (zonse) 
zimene mukuchita. 2 






ffijfc£*4&vfeb&\$%l 



®$%ffi 






Aya iyi ikufotokoza zakuletsedwa kukwatira akazi a Mtumiki (SAW), mwini 
wake atafa chifukwa choti akazi a Mtumiki(SAW) ndiamayi a Asilamu onse 
2 Pamene Mtumiki(SAW) adali mu mzinda wa Madina adamzinga magulu 
ambiri ankhondo omwe ena a iwo adali amtundu wa Ghatfan, Ayuda a 
Chikuraidha ndi Ayuda a Bani Nadhir. Adali ochuluka 12,000. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 21 I 889 I t \ *>i YT >->\y*H\ 3jj-- 



10. Pamene adakudzerani 
chakumtunda Kwanu, ndi kunsi 
kwanu (kumtunda Kwa dambo ndi 
kumunsi kwake), Pamene maso 
adangoti tong'oo Cham'mbali 
ndipo mitima idafika Kum'mero 
(chifukwa chamantha ndi 
Kunjenjemera) uku 
mukumganizira Mulungu 
maganizo osiyanasiyana. 

11. Panthawi imeneyo Asilamu 
adayesedwaMayeso aakulu. 
Adanj enj emeretsedwa 
Kunjenjemera kwambiri. 

12. Ndipo pamene ankanena 
Amunafikuna (Achinyengo) ndi 
omwe m' mitima Mwawo muli 
matenda: "Palibe chomwe 
Adatilonjeza Mulungu ndi 
Mtumiki Wake koma chinyengo 
basi." 

13. Ndipo pamene gulu lina 
mwa iwo lidanena: "E, inu nzika 
za mu Yathiriba (Madina)! Palibe 
njira kwa inu (yokhalira 
pankhondo Yogonjayi). Choncho 
bwererani (kunyumba Zanu; 















Pamene Mtumiki (SAW) adamva za kudza kwawo adakumba chidzenje 
chachikulu kumbali ina ya Mzinda wa Madina yomwe adaiganizira kuti adani 
angalowereko. Izi zidachitika potsatira malangizo a Salman Farisiyu. Kenako 
Mtumiki(SAW) adatuluka ndi ankhondo ake okwana 3,000 nakamanga 
mahema awo pafupi ndi chidzenjecho moyang'anizana ndi adani awo.Asilamu 
adagwidwa ndi mantha aakulu kotero kuti Asilamu achiphamaso adayamba 
kuthawa. Koma pompo Mulungu adatumizira adaniwo chimphepo ndi magulu 
ankhondo a angero omwe sadathe kuwaona ndi maso awo, nawabalalitsa 
adaniwo ndi kuwatayira katundu wawo kutali. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 21 



890 



y \ tj±\ rr ^\y*H\ ojj-- 



msiyeni Muhammad alimbane 
yekha Ndi adani ake)". Ndipo gulu 
lina lankhondo Lochokera mwa 
iwo limapempha chilolezo Kwa 
Mneneri(SAW) (Chobwerera ku 
Madina) ponena (kuti): "Ndithu 
nyumba zathu nzamaliseche 
(Zopanda chitetezo)". Koma izo 
Sizamaliseche. Sakufuna china, 
koma Kuthawabasi. 

14. Ndipo akadawalowera 
(magulu ankhondo A adaniwo), 
mbali zonse (za Mzindawo), 
Kenako nkupemphedwa kuti 
atuluke M'Chisilamu ndi 
kumenyana ndi Asilamu, 
Akadachita zimenezo; ndipo 
Sakadayembekezera koma nthawi 
yochepa Basi. 

15. Ndipo ndithu, (awa amene 
adathawa Pabwalo lankhondo), 
adali atamulonjeza Kale Mulungu 
(kuti iwo) sadzatembenuza Misana 
(kuthawa). Ndipo lonjezo la 
Mulungu nlofunsidwa. (Choncho 
Iwo adzafunsidwa pazomwe 
adalonjeza Kwa Mulungu). 

16. Nena: "Kuthawa 
sikungakuthandizeni Ngati 
mukuthawa imfa kapena 
Kuphedwa; choncho (kuthawa 
Kwanuku) simusangalatsidwa 
(nako) Koma pang'ono basi. 
(Kenako Ikatha nthawi yamoyo 
wanu, mukufa)". 



©!5& !^^wl s IS^^j 












Surat 33. Al-Ahzab Juzu 21 



891 



t y frjA-i rr ^\y*i\ *^ 



17. Nena: "Kodi ndani amene 
Angakutetezeni kwa Mulungu, 
Ngati atafuna kukuchitirani 
choipa; Kapena atafuna 
kukuchitirani chifundo?" Ndipo 
sadzapeza mthandizi ndi mtetezi 
Kupatula Mulungu. 

18. Ndithu, Mulungu 
akuwadziwa amene Akudziletsa 
mwa inu (kupita Kunkhondo 
pamodzi ndi Mtumiki (SAW), ndi 
Kuletsanso anthu ena). Ndi amene 
Akuuza abale awo:"Bwerani kwa 
ife; (M'thaweni 

Muhammad {SAW})." Ndiponso 
Sapita kunkhondo koma pang'ono 
Pokha. 

19. Okuchitirani inu umbombo 
(pachikondiNdi pachifundo; 
sakufunirani zabwino). Koma 
mantha akadza uwaona 
Akukuyang'ana, uku maso awo 
Akutembenuka 

(mophethiraphethira) Monga a 
amene wakomoledwa ndi Imfa. 
Koma mantha akachoka, 
Akukupatsani masautso ndi 
malirime Awo akuthwa; mbombo 
pa chabwino Chilichonse. Iwowo 
sadakhulupirire Ndipo choncho 
Mulungu wagwetsa Malipiro a 
zochita zawo. Zimenezo 
Nzosavuta kwa Mulungu. 

20. (Kufikira tsopano chifukwa 
cha mantha Awo) akuganiza kuti 












'\C 9 i'e\**< \' 9 \'X?sS\ '#'*'+ 



^$S^<&®G§& 



Surat33. Al-Ahzab Juzu 21 



892 



y \ *>t rr s-^ij^Vi 5jj- 



magulu ankhondo (Adani) 
sadapitebe; ndipo magulu Amenewo 
akadadzanso, akadalakalaka 
Akadakhala kuchipululu pamodzi 
ndi Anthu am'chipululu ndi kuti 
Azikangofunsa za nkhani Zanu. 
Akadakhala pamodzi ndi inu 
Sadakamenyana (ndi adani) koma 
Pang'ono pokha. 1 

21. Ndithu, muli nacho 
chitsanzo chabwino Mwa Mthenga 
wa Mulungu (M'kudzipereka 
kwake ndi khama Lake pa njira ya 
Mulungu, ndi kupirira Kwake ndi 
masautso) kwa yemwe Akuopa 
Mulungu ndi tsiku Lachimaliziro, 
namatchula Mulungu kwambiri. 

22. Ndipo pamene Asilamu 
adaona Magulu a nkhondo (a 
adani atawazinga Mbali 
zonse),adati: "Ichi ndichimene 
Mulungu ndi Mtumiki Wake 
Adatilonjeza (kuti tidzapeza 
masautso, Kenako nkupambana), 
ndipo Mulungu ndi Mtumiki Wake 
adanena zoona". Ndipo (ichi) 
sichidawaonjezere china, Koma 
chikhulupiriro (mwa Mulungu) 
Ndi kudzipereka. 






fan? 






Kuyambira ndime 12 mpaka 20, Mulungu akufotokoza makhalidwe a anthu 
ena amene adangolowa m'Chisilamu ndi lirime lokha pomwe mitima yawo 
siidakhulupirire. Nthawi zambiri ankamchitira Mtumiki (SAW) zachinyengo. 
Mtumiki (SAW) akalamula lamulo loti akalimbane ndi adani achipembedzo 
cha Chisilamu, iwo amagwetsa ulesi anthu kuti asapite kunkhondoko. Nthawi 
zambiri samawafunira Asilamu zabwino. Akangouzidwa kuti tiyeni kunkhondo, 
amagwidwa ndi mantha. 



Surat33. Al-Ahzab Juzu 21 



893 



t^ *>i 



rr ^yy 5jj-- 



23. Mwa okhulupirira alipo 
amuna ena Amene adakwaniritsa 
zomwe Adamlonjeza Mulungu 
(kuti Sadzathawa pankhondo 
pamodzi ndi Mtumiki{SAW}), ena 
mwa iwo adamaliza Moyo wawo 
(nakwaniritsa Lonjezo lawo pofera 
panjira ya Mulungu). Ndipo ena 
mwa iwo Akuyembekezerabe 
(kufera panjira ya Mulungu). Ndipo 
sadasinthe konse (Lonjezo lawo). 1 

24. Kuti Mulungu awalipire 
oona chifukwa Cha kuona kwawo; 
ndi kuti awalange Achiphamaso 
(Amunafikina) ngati Atafuna, 
kapena kuwalandira kulapa 
Kwawo (ngati atalapa). Ndithu, 
Mulungu Ngokhululuka kwabasi 
Ngwachisoni. 

25. Ndipo Mulungu 
adawabweza amene 
Sadakhulupirire uku ali odzazidwa 









£ 






1 Imamu Ibnu Jarir Taburiyu adalemba m'buku lake kuti Anasi Bun Malik 
adati:- M'bale wa bambo anga, Anasi bun Nadhari sadakhale nawo 
pankhondo ya Badri, ndipo adati: "Sindidakhale pamodzi ndi Mtumiki pankhondo 
yoyamba. Ngati Mulungu atandifikitsa pankhondo ina Mulungu adzaona 
zimene ndidzachita pomenya nkhondo modzipereka." Pa tsiku lankhondo ya 
Uhud, pamene Asilamu adabalalikana kuthawa ndipo iye adati:- "O.Ambuye 
Mulungu! Ine ndikudzipatula kuzomwe achita awa, osakhulupirira. Ndiponso 
ndikudandaula mzimene achita awa, Asilamu amene athawa." Kenako 
adayenda ndi lupanga lake akumana ndi Saad bun Muadhi, nati: "E, iwe 
Saad! Ine ndikumva fungo la ku Munda wa mtendere pafupi ndi phiri ili la 
Uhud." Kenako adachita nkhondo kufikira adaphedwa. Ndipo Saad adati: "E, 
iwe Mtumiki wa Mulungu! Sindinathe kuchita chimene iye adachita." Anasi bun 
Malik adati: Tidampeza ali m'gulu lophedwa uku ali ndi mabala okwanira 80, 
ena otemedwa ndi malupanga, ndipo ena olasidwa ndi mikondo ndi mipaliro. 
Sitidamzindikire kufikira pamene adadza mlongo wake naamzindikira 
pakupyolera m'nsonga za zala zake." Ndipo Anasi adatinso: "Tidali 
kukambirana kuti ndime iyi ikukamba za iye". 



Surat33. Al-Ahzab Juzu21 



894 



t \ ftjA-» rr ^yy «j>-< 



ndi Mkwiyo m'mitima mwawo; 
sadapeze Chabwino; (sadagonjetse 
Asilamu ndi Kupeza zimene 
ankaziyembekezera Monga zotola 
zapankhondo). Ndipo Mulungu 
adawakwaniritsira 
AsilamuNkhondo (powatumizira 
adani mphepo Yamkuntho ndi 
angero). Ndipo, Mulungu 
Ngwamphamvu, Ngopambana, 
(Sapambanidwa ndi chilichonse). 

26. Ndipo adawatsitsa 
m'malinga mwawo Amene 
adathandiza adaniwo mwa Anthu a 
Buku, (Ayuda). Ndipo adathira 
Mantha m'mitima mwawo. Ena 
Mumawapha; ndipo ena 
mumawagwira. ] 

27. Ndipo adakupatsani dziko 
lawo, Nyumba zawo, chuma 
chawo, ndi Nthaka imene 
simudaipondepo . Mulungu 
Ngokhoza chilichonse. 

28. E, iwe Mneneri! Nena kwa 
akazi ako (M'njirayowalangiza): 
"Ngati mufuna Moyo wadziko 
lapansi ndi zosangalatsa Zake (ine 
ndilibe zosangalatsa za M'dziko, 



mm& 






L if? 4. 



.Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupirira (akafiri) a 
Chiarabu ochokera mumtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi 
mapangano ndi Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) okhalirana 
mwamtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a 
Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, 
pomwe ena adawagwira monga akaidi apankhondo. 



Siirat33. Al-Ahzab Juzu 22 



895 



1 1 >jk\ rr <->\jrH\ 5jj~- 



ndipo sindingakukakamizeni Kuti 
mukhale ndi ine mumoyo 
Waumphawi; ngati mufuna) 
bwerani Ndikupatsani cholekanira, 
Chokusangalatsani, kenako 
ndikusiyeni Kusiyana kwabwino 
(kopanda Masautso). 

29. Ndipo ngati mukufuna 
Mulungu ndi Mtumiki Wake, ndi 
nyumba yomaliza, ndithu Mulungu 
wawakonzera ochita zabwino Mwa 
inu malipiro aakulu." 

30. E, inu akazi a Mneneri! 
Amene achite Choipa choonekera 
mwa inu, Amuonjezera chilango 
kawiri; ndipo Zimenezi nzosavuta 
kwa Mulungu 1 

31. Koma yense mwa inu 
amene amvere Mulungu ndi 
Mneneri Wake, ndi Kumachita 
zabwino ,timpatsa malipiro Ake 
kawiri ndi kumkonzera Riziki 
laulemu. 

32. E, inu akazi a Mneneri! Inu 
simuli Monga mmodzi wa akazi 
ena (omwe Siakazi a Mtumiki, 
paulemerero) ngati Muopa 












Mu aya imeneyi, akazi a Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
akuuzidwa kuti iwo akachimwa, Mulungu adzawalanga chilango chachikulu 
kuposa momwe akadalangidwira akazi ena omwe sali akazi a Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye). Izi nchifukwa chakuti, iwo ndi atsogeleri; 
chilichonse chomwe iwo achita, choipa kapena chabwino, chidzatsatidwa ndi 
ena. Akachita chabwino, Mulungu adzawapatsa malipiro aakulu. Ndipo 
akachita choipa, adzawalanga ndi chilango chachikulu. Choncho aliyense 
amene ndi mtsogoleri, aonetsetse kuti akuchita zolungama zokhazokha. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



896 



y y *>» rr <->\yH\ Sjj- 



Mulungu. Choncho Musalobodole 
mawu (mowakometsa 
Poyankhulana ndi amuna,) kuti 
Asalakelake (kuchita zoipa ndi 
inu) Yemwe mumtima mwake 
muli matenda (Achiwerewere). 
Koma nenani Zonena zabwino. 

33. Ndipo khalani m'nyumba 
zanu, ndipo Musadzionetsere (kwa 
amuna) uku Mutadzikongoletsa 
monga mmene Ankaonetsera 
zokongoletsa zawo (Akazi) a 
m'nthawi ya umbuli wakale. 
Ndipo pempherani swala 
moyenera; Perekani zakati; 
mverani Mulungu ndi Mtumiki 
Wake. Mulungu afuna 
Kukuchotserani uve. E, inu, 
akunyumba (Ya Mneneri!) Ndi 
kuti akuyeretsani ndithu. 

34. Ndipo lowezani pamtima 
zimene Zikunenedwa m'nyumba 
zanu; ndime Za Mawu a Mulungu 
ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa zinthu 
zobisika Kwambiri, ndi zapoyera. 

35. Ndithu, Asilamu achimuna 
ogonjera Mulungu mokwanira, ndi 
Asilamu Achikazi ogonjera 
Mulungu mokwanira; Okhulupirira 
achimuna ndi okhulupirira 
Achikazi; omvera achimuna ndi 
omvera Achikazi; oona achimuna 
ndi oona Achikazi; opirira 
achimuna ndi opirira Achikazi; 












Surat 33. AI-Ahzab Juzu 22 



897 



r r *>i rr ^y^ oj>- 



odzichepetsa achimuna ndi 
Odzichepetsa achikazi; opereka 
sadaka Achimuna ndi opereka 
sadaka achikazi; Osala achimuna 
ndi osala achikazi; Osunga 
umaliseche wawo (kuchiwerewere) 
Achimuna ndi osunga umaliseche 
wawo Achikazi; otamanda 
Mulungu kwambiri Achimuna ndi 
otamanda Mulungu Kwambiri 
achikazi, Mulungu Wawakonzera 
chikhululuko ndi Malipiro aakulu. 

36. Ndipo sikoyenera kwa 
wokhulupirira Wachimuna ndi 
wokhulupirira wachikazi, Mulungu 
ndi Mtumiki Wake akalamula 
Chinthu, iwo kukhala ndi chifuniro 
Pazinthu zawo. Ndipo amene 
akunyoza Mulungu ndi Mtumiki 
Wake, ndithu, Wasokera; kusokera 
koonekera. 1 

37. Ndipo (kumbuka) pamene 
udamuuza Yemwe Mulungu 
adampatsa mtendere 
(Pomuongolera ku Chisilamu, 
ndipo) Iwenso udampatsa 
mtendere (pomulera Ndi kumpatsa 
ufulu,yemwe ndi Zaid Bun 
Haritha, udati kwa iye): 
"Gwirizana ndi mkazi wako, ndipo 



© 












1 Ndime iyi ikunenetsa kuti sikoyenera kwa Msilamu kutsata maganizo ake 
pachlnthu chimene Mulungu ndi Mtumiki walamulapo lamulo, koma afunika 
kutsatira lamulo la Mulungu ndi Mtumiki, ndipo asakhale ndi chifuniro pa zinthu 
zomwe nza chipembedzo koma agonjere zimene Mulungu walamula ndi Mtumiki 
Wake. Kunyoza lamulo la Mulungu ndi Mtumiki kumachititsa kuti munthu atayike. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



898 



tt*>i rr oi^idj^ 



Opa Mulungu." Ukubisa mumtima 
Mwako chimene Mulungu afuna 
Kuchisonyeza poyera (chomwe ndi 
kuti Mulungu akulamula 
kumkwatira mkazi Ameneyo 
akamuleka Zaid Bun Haritha Kuti 
chichoke chizolowezi choti mwana 
Wongomulera chabe nkumuyesa 
Mwana wako weniweni). Ndipo 
ukuopa Anthu (kuti akudzudzula 
pazimenezo), Pomwe woyenera 
kumuopa ndi Mulungu. Choncho 
pamene Zaid adamaliza 
Chilakolako chake pa mkazi 
ameneyo, Tidakukwatitsa iwe kuti 
pasakhale Masautso pa Asilamu 
pokwatira akazi A ana awo 
akungowalera chabe ngati 
(Anawo) atamaliza zilakolako 
zawo pa Akaziwo, ndipo lamulo la 
Mulungu Ndilochitika,(palibe 
chingalepheretse Kuti lisachitike). 1 

38. Palibe tchimo pa Mneneri 
pa zimene Mulungu wamulamula. 
Chimenechi Ndichizolowezi cha 
Mulungu (njira ya Mulungu) pa 
amene adanka kale. Ndipo Lamulo 
la Mulungu ndi chiweruzo 









Polamula chinthu kuti chichitike kapena chisachitike, pafunika kuti iwe 
wolamula ukhale woyamba kutsata malamulowo. Ngati sutero, ndiye kuti 
malamulo akowo sangakhale ndi mphamvu. Mu ndime iyi ,muli lolezo 
lakumkwatira mkazi yemwe wasiyidwa ukwati ndi mwana yemwe 
adangoleredwa chabe ndi munthu amene amatcha mwanayo kuti ndi mwana 
wake chifukwa chomulera. Kalelo zoterezi sizimaloledwa. Choncho Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) adauzidwa kuti achite iye mwini 
zimenezi pofuna kuthetsa chikhalidwecho. 



Surat 33. AI-Ahzab Juzu 22 



899 



y t fr>» rr *->\y*H\ ijy* 



(Chomwe) chidaweruzidwa. 
(Ndipo sichisinthidwa). 1 

39. (Aneneri) amene amafikitsa 
uthenga wa Mulungu (kwa anthu) 
uku akumuopa lye, ndipo 
samamuopa aliyense koma 
Mulungu (yekha). Ndipo Mulungu 
Akukwana kukhala wowerengera 
(Zochita za akapolo Ake). 

40. Muhammad (SAW) sali tate 
wa aliyense mwa Amuna anu, 
koma iye ndi Mtumiki wa 
Mulungu, ndiponso wotsiriza mwa 
Aneneri. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa Chilichonse. 

41. E, inu amene 
mwakhulupirira! Tamandani 
Mulungu; kumtamanda Kwambiri; 

42. Ndipo mulemekezeni 
m'mawa ndi madzulo. 









&Q&&£ffi&&%& 



&M&*j&3$& 



V ( j»», 



©1 



e5M5tS*>¥/ 



1 Ndime iyi ikumuuza Mtumiki (SAW) kuti palibe vuto pa iye ngakhale tchimo 
kapena kudzudzulidwa pachomwe Mulungu wamulamula kuchichita monga 
kukwatira akazi ambiri. Ayuda amamunyoza ndi kumudzudzula chifukwa 
chokwatira akazi ambiri. Koma Mulungu adawayankha ndi mawu ake oti, "Iyi 
ndi njira ya Mulungu yomwe idalipo pa Aneneri akale! Daudi adakwatira akazi 
100. Ndipo Sulaimani akazi 300. 

2 Ndime iyi ikumuuza Mtumiki kuti amene adamulamula kuti awatsanzire 
pazimene ankachita ndi iwo amene ankafikitsa uthenga wa Mulungu kwa 
anthu, ndipo samaopa kudzudzulidwa ndi aliyense pachomwe Mulungu 
wawalamula kuchita, koma ankangoopa Mulungu yekha. Choncho nawenso 
tsanzira khalidwe lawo ndi kuopa Mulungu yekha. 

3 ("Khataman Nabiyyina) "Mneneri wotsirizira" tanthauzo lake ndi kuti Mtumiki 
Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndimneneri womalizira; 
palibe mneneri wina pambuyo pake mpaka kutha kwadziko lapansi. Aya 
imeneyi ikutsutsa ndi zonena za Akadiyani omwe akumutcha mtsogoleri wawo 
kuti ndi mneneri. 

4 Mulungu wasankha nthawi ziwiri kuti zikhale zochulukitsa kumtamanda ndi 
kumulemekeza chifukwa chakuti zimenezi ndi nthawi zabwino zimene angelo 
amatsika kuchokera kumwamba. 



Surat 33, Al-Ahzab Juzu 22 



900 



t y ^>i rr ^\j^H\ djj- 



43. lye ndi Amene 
akukuchitirani chifundo(Ndi 
kukufunirani zabwino) nawonso 
Angero Ake (akukupemphererani 
kwa Mulungu) kuti akutulutseni 
mumdima Ndi kukuikani 
m'kuunika. Ndipo (lye) 
Ngwachisoni kwa Asilamu. 

44. Kulonjerana kwawo tsiku 
lokumana Naye, kudzakhala koti: 
"Mtendere!", Ndipo wawakonzera 
malipiro a ulemu. 

45. E, iwe Mneneri (wa 
Mulungu)! Ndithu, Ife takutuma 
(kuti ukhale) mboni (pa Anthu ako 
ndi pamibadwo yonse).Wonena 
Nkhani zabwino (kwa oopa 
Mulungu), Ndi mchenjezi (kwa 
onyoza Mulungu). 

46. Ndi kuti ukhale woitanira 
(anthu) kwa Mulungu kupyolera 
m'chifuniro Chake. Ndi (kutinso 
ukhale) nyali younikira (Anthu). 

47. Ndipo auze nkhani yabwino 
okhulupirira Kuti iwo ali ndi 
zabwino zazikulu kwa Mulungu. 

48. Ndipo usawamvere 
osakhulupirira ndi Achiphamaso 
(pazimene akufuna kuti 
Uwapeputsire malamulo a 
Mulungu), Usalabadire masautso 
awo, ndipo tsamira Kwa Mulungu. 
Ndipo Mulungu Akukwanira 
kukhala Mtetezi. 









eg^^f&MW 









Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



901 



y v t>i rr ^\y-H\ *>^> 



49. E, inu amene 
mwakhulupirira! Mukakwatira 
akazi okhulupirira, kenako 
Ndikulekana nawo 
musadawakhudze, Inu mulibe 
chiwerengero cha 'edda' Pa iwo 
choti nkuchiwerengera. 
Asangalatseni powapatsa 
cholekanira, Siyananawoni; 
kusiyana kwabwino. 

50. E, iwe Mtumiki! Ndithu Ife 
takuloleza (Kukhala nawo 
pamodzi) akazi ako Amene 
wawapatsa chiwongo chawo, Ndi 
chimene dzanja lako lamanja 
Lapeza (omwe ndi akazi ogwidwa 
Pankhondo) chomwe Mulungu 
Wakupatsa, ndi ana achikazi a 
m'bale wa Atate ako, ndi ana 
achikazi a mlongo Wa atate ako, 
ndi ana achikazi a Atsibweni ako, 
ndi ana achikazi a m'bale Wa mayi 
ako amene adasamuka pamodzi 
Ndi iwe, ndi mkazi wachisilamu 
Atadzipereka yekha kwa Mneneri 
ngati Mneneri akufuna 
kumkwatira, chilolezo Ichi ncha 
iwe wekha, osati Asilamu Onse. 
Ndithu, tafotokoza malamulo 
Amene tawakhazikitsa kwa iwo pa 



1 'Edda' ndi nthawi imene mkazi amakhala pachiyembekezero asanakwatiwe 
ndi mwamuna wina pambuyo posiyana. Edda zilipo za mitundu iwiri: yosiyana 
ukwati yomwe mkazi amayembekezera miyezi itatu ndi yomwalira mwamuna 
yomwe mkazi amayembekezera miyezi inayi ndi masiku khumi. Koma mkazi 
wapakati Edda yake imatha ndikubereka. Yang'anani ndemanga ya Qur'an 
(2:228). 









Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



902 



r r ^>i rr ^\y^H\ '^^ 



Akazi awo, ndi chimene manja 
awo Akumanja apeza; (takuchitira 
zimenezi iwe Wekha Mneneri 
Muhammad {SAW}) kuti 
Pasakhale masautso pa iwe (ngati 
ukufuna Kukwatira mkazi wina 
chifukwa Chofalitsa chipembedzo) 
ndipo Mulungu Ngokhululuka 
kwambiri Ngwachisoni. 

51. Ukhoza kumchedwetsa 
(posagona M'nyumba mwake) 
amene wam'funa Pakati pa iwo ndi 
kumuyandikitsa kwa Iwe amene 
wam'funa. Ndipo amene 
Wam'funa mwa amene 
udawapatuka, Palibe tchimo pa 
iwe. Kuchita izi Kuchititsa kuti 
maso awo atonthole (Mitima yawo 
ikondwe) ndipo Asadandaule;ndi 
kuyanjana nacho chimene 
Wawapatsa onse. Ndipo Mulungu 
Akudziwa zimene zili m'mitima 
Mwanu. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa Kwambiri, Ngoleza, 
(salanga Mwachangu). 

52. Pambuyo (pa akazi awa 
amene uli nawo) Nkosaloledwa 
kwa iwe kukwatira akazi Ena, 
(poonjezera pachiwerengero cha 
akazi Amene uli nawo). Ndiponso 
usasinthe (Ofanana ndi 
chiwerengero chawo), (Zonsezi 
nzoletsedwa kwa iwe) ngakhale 
Kuti ubwino wawo 
utakusangalatsa, Kupatula chimene 









S u rat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



903 



XT frjJH 



TT ^Ij^-Sl *jj~> 



dzanja lako lakumanja Lapeza; 
Ndipo Mulungu ndimlonda 
Wachinthu chilichonse. 

53. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musalowe 
m'nyumba za Mneneri 
Pokhapokha chilolezo 
Chitaperekedwa kwa inu kukadya, 
osati Kukhala nkuyembekezera 
kupsa kwa Chakudya. Koma 
mukaitanidwa, Lowani. Ndipo 
mukamaliza kudya, Balalikanani; 
ndiponso musakambe Nkhani 
zocheza. Chifukwa kutero 
Kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye 
Amakuchitirani manyazi (kuti 
Akutulutseni); koma Mulungu 
alibe Manyazi ponena choona. 
Ndipo inu Mukamawafunsa (akazi 
ake) za ziwiya, Afunseni uku muli 
kuseri kwa Chotsekereza. Kuchita 
zotere, kuyeretsa Mitima yanu ndi 
mitima yawo. Sikoyenera kwa inu 
kumvutitsa Mtumiki wa Mulungu, 
ndiponso Nkosayenera kwa inu 
kukwatira akazi Ake pambuyo pa 
imfa yake mpaka Muyaya. Ndithu, 
kutero ndi tchimo Lalikulu kwa 
Mulungu. 1 






Anasi(RA) adanena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha anthu ena omwe 
ankangocheza m'nyumba ya Mtumiki(SAW), osatulukamo. Izi zidali motere: 
Pamene Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adakwatira Zainabu 
Binti Jahashi, adachita phwando la chakudya ndipo adaitana anthu. Pamene 
adatha kudya ena a iwo adangokhala nkumacheza m'nyumba ya Mtumiki 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye). Pamenepo nkuti mkazi wake 
atayang'anitsa nkhope yake kukhoma la nyumba. Zoterezi zidamuvuta 
Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti awatulutse m'nyumbamo. 
Apa mpamene Mulungu adavumbulutsa ndimeyi. 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



904 | tt *>i tr yjj^i 5jj^ 



54. Chilichonse chimene 
mungachionetse Kapena kuchibisa, 
(Mulungu achidziwa, Ndithu) 
chifukwa chakuti Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 

55. Palibe tchimo pa iwo 
(akazi) kuonana Ndi atate awo 
ngakhale ana awo, alongo Awo, 
ana amuna alongo awo, ana a 
Amuna a abale awo, akazi anzawo, 
Ndi amene manja awo akumanja 
apeza. Ndipo opani Mulungu (inu 
akazi). Ndithu, Mulungu ndimboni 
pa chilichonse. 

56. Ndithu, Mulungu 
akumtsitsira madalitso Mtumiki 
Wake; nawonso angero Ake 
(Akumphempherera chifukwa cha 
Zochita zake zabwino). E, inu 
amene Mwakhulupirira! 
Mpemphereni Madalitso ndi 
kumpemphera mtendere (Chifukwa 
chokusonyezani njira Yolungama). 

57. Ndithu, amene akukwiyitsa 
Mulungu Ndi kuvutitsa Mtumiki 
Wake (ponyozera Malamulo ake) 
Mulungu Wawatemberera padziko 
lapansi(Mpaka) pa tsiku la 
chimaliziro, ndipo Wawakonzera 
chilango chosambula. 

58. Ndipo amene akuvutitsa 
Asilamu Aamuna ndi Asilamu 
aakazi popanda Kuchimwa 
kulikonse, ndithu, Achisenza 
chinyengo ndi tchimo Loonekera. 















&C*"** 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 



905 y t tj±\ rr ^>\^H\ t^ 



59. E, iwe mneneri! Uza akazi 
ako, ndi ana Ako aakazi, ndi akazi 
a Asilamu, kuti Adziphimbe ndi 
nsalu zawo (Akamatuluka 
m'nyumba), kutero Kuchititsa kuti 
adziwike, asazunzidwe (Ndi anthu 
achipongwe). Ndipo Mulungu 
Ngokhululuka Kwambiri 
Ngwachisoni. 

60. Ngati sasiya (machitidwe 
awo oipa) (Amunafikina) 
achinyengo, ndi amene Ali ndi 
matenda m'mitima mwawo 
(Achiwerewere), ndi ofalitsa mbiri 
Zoipa mumzinda, tikukhwirizira 
kwa I wo (kuti uwathire nkhondo). 
Kenako Sadzakhala m'menemo 
pamodzi ndi iwe, Koma nthawi 
yochepa. 

61. (Iwo) ngotembereredwa; 
paliponse Pamene apezeke, 
agwidwe ndi Kuphedwa, ndithu. 

62. (Awa ndi) machitidwe a 
Mulungu omwe Adalipo pa omwe 
adamka kale. Sungapeze kusintha 
Pamachitidwe a Mulungu. 

63. Anthu akukufunsa za (kudza 
kwa) nthawi (Ya tsiku la 
chitsiriziro). Nena: "Kuzindikira 
kwa nthawiyo kuli ndi Mulungu 
(yekha). Nanga nchiyani 
Chikudziwitse kuti nthawi ya 
chimaliziro Iri pafupi? 






»-fr»f '.ii. k <f » «' 



$jK>Sa^( 



V>1 



®%?£&&\&?(g$% 









Surat 33. AI-Ahzab Juzu 22 906 t T *>» TT *-^SM ojj~- 



64. Ndithu, Mulungu 
wawatemberera Osakhulupirira ndi 
kuwakonzera moto Woyaka 
kwambiri; 

65. Adzakhala m'menemo 
muyaya. Sadzapeza bwenzi 
Ngakhale mthandizi. 

66. Tsiku limene nkhope zawo 
Zikatembenuzidwa ku moto 
(Zikutenthedwa), uku akunena: 
"Kalangaife! Tikadamumvera 
Mulungu Ndi kumveranso 
Mtumiki(SAW), (sibwenzi Tili 
m'chilangomu)" 

67. Ndipo adzanena: "O, Mbuye 
wathu! Ndithu, ife tidamvera 
olemekezeka athu, Ndi akuluakulu 
athu, choncho Adatisokeza njira. 

68. Mbuye wathu! Apatseni 
chilango Pamwamba pa chilango 
ndipo Atemberereni, kutemberera 
Kwakukulu." 

69. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musakhale 
monga amene adamvutitsa Musa; 
koma Mulungu adamuyeretsa 
Kuzimene ankamnenera. Ndipo iye 
Kwa Mulungu adali wolemekezeka. 1 



^^a^t^i^^a 



'>\>l' Mil 1 *9>*>f 9&.1"' 






% 



©!£|EJ 



1 M'ndime iyi, Mulungu akulangiza Asilamu kuti asamuvutitse Mtumiki ndi 
kumnenera mawu opanda ulemu monga momwe Ayuda ankamunenera Musa 
Ana a Israeli adamunamizira Musa kuti ali ndi khate pathupi lake, kapena kuti 
ali ndi matenda a mwera (phudzi). Koma Mulungu adamuyeretsa kuzomwe 
adali kumunamizirazo. Adamuyeretsa motere monga momwe Bukhari 
akunenera muhadisi yomwe idalandiridwa kuchokera kwa Abu Huraira (RA) 
kuti Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) adati: Musa adali munthu 



Surat 33. Al-Ahzab Juzu 22 I 907 I tt *>» YT ^»\yH\ 5j>* 



70. E, inu amene 
mwakhulupirira! Opani Mulungu 
(pokwaniritsa Malamulo Ake, ndi 
kusiya zoletsedwa), Ndipo nenani 
mawu olungama, 

71. Akukonzerani bwino zochita 
zanu ndi Kukukhululukirani 
machimo anu. ndipo amene 
akumvera Mulungu ndi Mtumiki 
Wake, ndithu, apambana; 
kupambana kwakukulu. 

72. Ndithu, Ife tidapereka 
malamulo athu Kuthambo ndi 
nthaka ndi mapiri; koma Zidakana 
kuwasenza (malamulowo); ndipo 
Zidawaopa. Koma munthu 
adawasenza; Ndithu, iye 
ngwachinyengo kwambiri 
Ndiponso mbuli. 

73. Kuti Mulungu adzawalange 
achinyengo Aamuna ndi aakazi, ndi 
opembedza Mafano achimuna ndi 
achikazi ndi kuti Adzawakhululukire 
Asilamu achimuna Ndi achikazi. 
Ndipo Mulungu Ngokhululuka 
kwabasi, Ngwachisoni. 



\py&\\&\PY£0$% 



'■* 'A*4 






'(s 



:-,v'4i»,i»rxi«r>^ 









wamanyazi, ndipo amabisa thupi lake. Khungu lake silimaoneka chifukwa cha 
manyazi ake. Ndipo adamuvutitsa ena mwa ana a Israeli. Adati: 
"Sangadzibise motere koma khungu lake pali chochititsa manyazi, mwina 
khate kapena matenda amphepo yamwera (phudzi), kapena matenda ena 
aliwonse!" Ndipo Mulungu adafuna kumuyeretsa kuzimene ankamunamizirazo. 
Tsiku lina Musa adakhala payekha navula nsalu zake naika pamwala. Kenako 
adayamba kusamba. Pamene adamaliza kusamba adacheukira komwe 
adaika nsalu zake kuti azitenge Adaona mwala ukuthawitsa nsalu zake. Musa 
adatenga ndodo yake nkumathamangira mwalawo uku akunena: "Nsalu zanga, 
iwe mwala! Nsalu zanga iwe mwala!" Mpaka adadutsa pomwe adakhala 
akuluakulu a ana alsraeli namuona thupi lake lili losalala kwabasi; lopanda 
chilema chilichonse. Potero Mulungu adamuyeretsa kuzomwe ankamunenerazo. 



Surat 34. Saba' Juzu 22 



908 tt *j*-» rt L-«j>- 




Sura yolemekezekayi yayamba ndi kulemekeza Mulungu 
Yemwe adayambitsa zolengedwa ndi kulongosola zinthu Zake 
zam'dziko zakuya. lye ndi Mlengi Wanzeru zakuya Yemwe 
palibe chimene chingabisike kwa lye m'kudziwa Kwake, 
ngakhale kachinthu kolemera monga nyerere muthambo ndi 
m'nthaka. Ndipo ichi nchisonyezo chachikulu chosonyeza 
umodzi wa Mbuye wazolengedwa. 

Surayi yafotokoza nkhani yaikulu kwambiri yomwe ndi 
kusakhulupirira kwa opembedza mafano pa tsiku la chimaliziro 
ndi kutsutsa kwawo zakuuka kuimfa. Ndipo yalamula Mtumiki 
kuti alumbirire kwa Mbuye wake Wamkulu potsimikiza kuti 
ndithu, kuuka kuimfa kulipo pambuyo poonongeka matupi. 

Yafotokozanso nkhani za aneneri ena; yafotokoza za Daudi 
ndi mwana wake Sulaiman (mtendere wa Mulungu ukhale pa 
iwo) ponena kuti Mulungu adawadalitsa ndi madalitso ambiri 
monga kumgonjetsera mphepo Mneneri Sulaiman kuti 
imtumikire, monganso kumgonjetsera mbalame ndi mapiri 
Mneneri Daudi kuti zikhale zikuthandizana naye polemekeza 
Mulungu, ndi madalitso ena ambiri. 

Surayi yafotokozanso maganizo a opembedza mafano ndi 
okaikira uthenga wa Mtumiki Muhammad (mtendere wa 
Mulungu ukhale pa iye). Ndipo yapereka mitsutso yothetsa 
chikaiko chawocho. Ndipo Surayi yamaliza ndi kuitana opembedza 
mafano kuti akhulupirire Mulungu mmodzi wamphamvu Yemwe 
m'manja Mwake muli chikonzero cha chinthu chilichonse. 




Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



909 



TT frjA-i 



T t t-*» 0j j-*» 



S«ra/Sa6a'AXX7K 




M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuyamikidwa kwaulemu 
nkwa Mulungu Yemwe 
zakumwamba ndi Zapansi 
nzake.Ndipo kutamandidwa Konse 
kwaulemu pa tsiku lomaliza 
Nkwake. ndiponso lye Ngwanzeru 
Zakuya, Ngodziwa chilichonse. 

2. Akudziwa zimene zikulowa 
m'nthaka Ndi zimene 
zikutulukamo; ndi zimene 
Zikutsika kumwamba ndi zimene 
Zikukwera kumeneko.Ndipo lye 
Ngwachifundo kwabasi, 
Ngokhululuka kwambiri. 1 

3. Ndipo osakhulupirira 
adanena: "Siizatidzera nthawi 
(Kiyama)." Nena: "lyayi! 
Ndikulumbira Mbuye Wanga, 
ndithu, ikudzerani. (Mbuye 
Wanga) Wodziwa zobisika 
(zonse), Sichingabisike kwa lye 
cholemera ngati Nyerere; 
chakumwamba,chapansi Ngakhale 
chochepa kuposa Chimenecho; 
ngakhale chokulirapo, Koma 



o&g\&3\&\j 



^ 









fa J *!. J.C* 



-V •* 'W 



1 M'ndime iyi Mulungu akutidziwitsa kuti akudziwa zonse zimene zikulowa 
m'nthaka monga madzi, mitembo ndi zina zotero. Ndipo akudziwanso zimene 
zikutuluka m'menemo - monga mmera tizirombo, miyala yamtengo wapatali 
ndi madzi. Ndi zomwe zikutsika kumwamba monga mvula, matalala, mphenzi, 
madalitso, angero Ake ndi mabuku Ake. Ndipo akudziwanso zimene 
zikukwera kumwamba - monga ntchito za akapolo Ake ndi zina zotero. 



Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



910 



yy frj*-i 



ft U 5 j j-j 



(zonsezo) zili m'Buku (Lake) 
Losonyeza poyera (chilichonse). 

4. Kuti adzawalipire amene 
akhulupirira Ndi kuchita zabwino; 
iwo adzapeza Chikhululuko ndi 
zopatsidwa zaulemu." 

5. Koma amene alimbika 
kutsutsana ndi Aya zathu 
pomaganiza kuti Atigonjetsa, pa 
iwo pali chilango Chopweteka. 

6. Koma amene apatsidwa 
(dalitso la) Kudziwa akuzindikira 
kuti zimene Zavumbulutsidwa kwa 
i we kuchokera Kwa Mbuye wako 
nzoona, Ndipo zikuongolera ku 
njira ya Mwini Mphamvu zoposa; 
Wotamandidwa. 

7. Ndipo osakhulupirira 
akunena (pouzana Pakati pawo 
mwachipongwe): "Kodi 
Tikusonyezeni zamunthu yemwe 
Akukuuzani kuti (m'kadzafa) ndi 
Kudukaduka m'dzakhala 
m'chilengedwe Chatsopano?" 

8. (Mulungu akunena): "Kodi 
(Akum'ganizira Muhammad kuti) 
Wapekera Mulungu bodza, kapena 
Wagwidwa ndi misala? Iyayi, 
koma Osakhulupirira za tsiku la 
chimaliziro Adzakhala m' chilango 
ndi m'kusokera Kwakukulu. 

9. Kodi (agwidwa ndi khungu) 
saona Zomwe zili patsogolo pawo 
ndi Pambuyo pawo monga thambo 






**•• 















Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



911 



rr *>i 



V* t l--»» * j j-*i 



ndi Nthaka (kuti adziwe kukhoza 
Kwathu Kuchita zimene tafuna)? 
Tikadafuna Tikadawakwirira ndi 
nthaka kapena Kuwagwetsera 
zidutswa za thambo. Ndithu, 
m'zimenezo muli malingaliro Kwa 
kapolo aliyense wotembenukira 
(Kwa Mulungu). 

10. Ndithudi, Daudi tidampatsa 
chisomo Chachikulu chochokera 
kwa Ife. (Ndipo Tidauza mapiri 
kuti akhale akuvomereza 
Mapemphero a Daudi 
pothandizana Naye. Tidati): "E,inu 
mapiri pamodzi Ndi iye Daudi, 
lemekezani (Mulungu), Ndi inunso 
mbalame." Ndipo 
Tidamufewetsera chitsulo. 

11. (Tidati kwa iye:) "Panga 
zovala (Zachitsulo) zophanuka 
(zokwana thupi Lonse, 
zodzitetezera pa nkhondo), Ndipo 
linga bwino m'kulumikiza ndi 
Poluka. Potero chitani zabwino, 
(ee, inu Akubanja la Daudi!). 
Ndithu, Ine Ndikuona zonse 
zimene mukuchita." 1 

12. Nayenso Sulaiman 
tidamgonjetsera Mphepo (yomwe 
inkayenda mwa Lamulo lake). 



V**'"' * • 












1 Mulungu Wapamwambamwamba adamfewetsera Daudi chitsulo kotero kuti 
adachisungunula nkusanduka ngati phala, napanga kuchokera m'phala 
limenelo zovala zodzitetezera pankhondo, ndiponso ziwiya zina zothandiza pa 
umoyo. Ichi chidali chisomo chachikulu chimene Mulungu adamdalitsa nacho 
iye pamodzi ndi ife tonse. 



Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



912 



tt *>i 



T i t—» o jj-»> 



Mayendedwe amphepoyo 
Inkayenda kuyambira m'mawa 
mpaka Masana mtunda wofanana 
ndi waulendo Wa mwezi umodzi; 
Ndiponso Kuyambira masana 
mpaka madzulo Inkayenda mtunda 
wofanana ndi Waulendo wamwezi 
umodzi. Ndipo Tidamsungunulira 
kasupe wamtovu. Ndiponso 
m'ziwanda (majini) Zidaliponso 
zimene tidam'gonjetsera Zomwe 
zinkam'gwirira ntchito 
Mwachilolezo cha Mbuye wake 
(Mulungu). Ndipo yense mwa iwo 
Wonyoza lamulo Lathu (Posiya 
kumumvera Sulaiman) Timulawitsa 
chilango cha moto woyaka. 

13. Ziwandazi zimampangira 
zimene Wafuna, monga: misikiti, 
zithunzi Zokhala ndi matupi, ndi 
mabeseni onga Madamu ndi 
midanga Yokhazikika. 
(Tidawauza:) "Chitani Ntchito 
zabwino, E, inu akubanja la Daudi 
pothokoza (madalitso amene 
Mwapatsidwa). Komatu ndiochepa 
Othokoza mwa akapolo Anga" 

14. Pamene tidalamula imfa 
yake (Sulaiman), palibe chimene 
Chidawasonyeza za imfa yake 
koma Kachirombo kam'nthaka 
(chiswe) Kamene kadadya ndodo 
yake. Choncho Pamene adagwa, 
ziwanda zidazindikira Kuti 
zikadakhala zikudziwa zobisika 












Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



913 "*>» 



Tt L»» 5 j y> 



Sizidakakhala m'chilango 
Chosambulacho. 1 

15. Ndithu, padali phunziro pa 
anthu A dziko la Saba mokhala 
mwawo: (Padali) minda iwiri, 
Kumanja ndi kumanzere. (Tidati:) 
"Idyani riziki (zaulere) Lochokera 
kwa Mbuye warm, ndipo 
Mthokozeni. Mudzi wabwino ndi 
Mbuye Wokhululuka. 

16. Koma adanyozera (lamulo 
la Mulungu); choncho 
tidawatumizira Chigumula 
champhamvu (chomwe 
Chidawamiza ndi kuononga minda 
Yawo). Ndipo tidawasinthira 
Minda yawo (yabwino) kukhala 
minda Iwiri yazipatso zowawa, ndi 
mitengo Ya isili (yomwe 
chikhalirenicho ndi Yosabereka 
zipatso,) ndi mitengo Pang'ono ya 
masawu. 2 






*»i< 

®jj*> 






1 Kalelo anthu adali ndi chikhulupiriro chakuti ziwanda zimadziwa zamseri; 
monga kudziwa zam'tsogolo. Ndipo kudapezeka kuti Sulaiman adaimirira 
kupemphera ku chipinda chake chopempherera uku atatsamira ndodo yake, 
imfa niimpeza ali chiimirire, choncho adakhala chaka chathunthu ali 
chomwecho uku atafa kale. Mmenemo nkuti ziwanda zikugwira ntchito 
yotopetsa, osadziwa kuti Sulaiman adafa, mpaka pamene chiswe chidadya 
ndodo imene adatsamira, nagwa pansi. Apo mpomwe imfa yake idadziwika. 
Potero anthu adadziwa tsopano kuti ziwanda sizidziwa zam'tsogolo. 

2 Anthu am'mudzi wa Saba'a komwe nkudziko la Yemeni, Mulungu 
adawapatsa madalitso ambiri pamene iwo amatsatira malamulo Ake ndi 
kumthokoza. Adawadalitsa ndi minda ya zipatso zokoma zomwe zidalibe 
nyengo yeniyeni yobalira, kotero kuti azimayi ankangosenza madengu 
nkumangoyenda pansi pa mitengo ndipo mwadzidzidzi ankangoona madengu 
ali odzaza ndi zipatso zoyoyoka m'mitengoyo. Koma pamene adasiya 
kuyamika Mulungu ndi kutsatira malamulo Ake, adawaonongera mindayo ndi 
chigumula ndi kuwasinthitsira zipatso zawo ndi zipatso zopanda pake. 



Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



914 



tt *>i 



Ti t-*» 5jj-*» 



17. Amenewo ndiwo malipiro 
omwe Tidawalipira chifukwa cha 
Kusathokoza kwawo (Mtendere 
wa Mulungu). Ndipo Ife sitilipira 
zoterezi koma Kwa okhawo 
osathokoza. 

18. Ndipo pakati pawo ndi 
pakati pamidzi Imene tidaidalitsa, 
tidaikapo midzi Imene idali 
yoonekera; ndipo tidapima 
M'menemo malo 

apaulendo.(Kotero Kuti amachoka 
malo nkufika malo Ena 
mosavutika. Tidawauza): 
"Yendani M'menemo usiku ndi 
usana Mwamtendere." 

19. Koma (adauda mtendere 
umenewu;) Adati: "O, Mbuye 
wathu! Talikitsani mtunda pakati 
pa maulendo Athu; (kuyandikirana 
kwa midzi, Sikukutisonyeza kuti 
tili paulendo);" Choncho 
adadzichitira okha zoipa. Ndipo 
tidawachita kukhala Miyambi 
(imene anthu a pambuyo 
Ankauzana pakati pawo), ndipo 
Tidawabalalitsa; kubalalikana zedi. 
(Ena adathawira dziko ili, ena dziko 
lina). Ndithu, m'zimenezo muli 
Malingaliro kwa yense wopirira 
Kwabasi ndi wothokoza kwambiri. 

20. Ndipo ndithu, Iblis 
adatsimikiza Ganizo lake pa iwo 
choncho Adamtsatira kupatula 
Gulu la okhulupirira (moona). 












99?"$?'; <{ji/ 9>\?\ 9 *\' <.<&'' *'\" 



Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



915 l*Y»>i 



V t L-*» 3 j j-»» 



•• 









21. Ndipo iye adalibe nyonga 
pa iwo, koma Chifukwa chakuti 
tionetse poyera ndani 
Wokhulupirira tsiku lachimaliziro 
Ndiponso ndani amene 
akulikaikira. Ndipo Mbuye wako 
Ngosunga chilichonse. 1 

22. Nena: "Itanani amene 
mukuwatcha kuti Ndi milungu 
kusiya Mulungu (kuti 
Akuthandizeni. Koma 
Sangakuthandizeni chilichonse; 
Pakuti iwo) alibe ngakhale 
kachinthu Kakumwamba ndi pansi 
kolemera ngati Nyerere yaing'ono 
kwambiri; M'menemo iwo alibe 
gawo lililonse (Lothandizana ndi 
Mulungu), Ndipo ngakhale Iyenso 
alibe mthandizi Wochokera mwa 
iwo. 

23. Ndipo uwomboli 
sudzathandiza kwa Iye (Mulungu) 
kupatula amene Wamuloleza." 
Choncho (zikatero) kuti,Pamene 
mantha adzachotsedwa M'mitima 
mwawo (popatsidwa Chilolezo 
choti apulumutse ena), Adzanena 
pakati pawo (mosangalala): "Kodi 
wanena chiyani Mbuye wanu?" 
(Adzayankha), "Ndithu, Iye wanena 
choona; Iye Ngotukuka Ngwamkulu. 



Pamene satana adatha kumsokeretsa Adamu adaganizanso kuti adzatha 
kuwasokeretsa ana ake. Ndipo ana a Adamu adamtsatiradi satanayo monga 
momwe iye ankaganizira. Komatu satana alibe mphamvu zomkakamizira mwana 
wa Adamu kuti amtsate koma amangomuitana kupyolera m'kukometsera 
ziiakolako zoipa. 






Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



916 



TT tj)r\ 



T t L— » 5 j j-» 



24. Nena (kwa iwo, iwe 
Mneneri{SAW}): "Kodi Ndani 
amakupatsani riziki (zaulere) 
Kuchokera kumwamba ndi pansi?" 
(Ngati sakuyankha chifukwa 
Chodzitukumula), nena (kwa iwo): 
"Ndi Mulungu (mmodzi, amene 
Akukupatsani zopatsa zaulere 
Zochokera kumwamba ndi 
pansi);Ndipo ife kapena inu, tili 
pachiongoko Kapena mkusokera 
koonekera" 

25. Nena: "Simudzafunsidwa 
pazolakwa Zimene (ife) talakwa, 
nafenso Sitidzafunsidwa pazimene 
mukuchita." 

26. Nena (kwa iwo): "Mbuye 
wathu Adzatisonkhanitsa pakati 
pathu (Pa tsiku la chiweruzo). 
Kenako Adzaweruza pakati pathu 
Mwachoonadi; lye ndi Muweruzi 
Wodziwa kwambiri." 

27. Nena (kwa iwo): 
"Ndisonyezeni amene 
Mwawalumikiza ndi lye monga 
Othandizana naye; Iyayi, 
sizingatheke (lye kukhala ndi 
anzake) koma lye (Yekha) ndiye 
Mulungu, Mwini Mphamvu 
zoposa, Wanzeru zakuya." 

28. Ndipo sitidakutumize (iwe, 
Mtumiki{SAW} Kwa Arabu okha) 
koma kwa anthu onse, kuti ukhale 
wouza okhulupirira Nkhani 






.? 4 \\i 



iJP$$^\&v$£5$& 



*&^0®ZS&$ 



©Z&\pB& 









Siirat 34. Saba' 



Juzu 22 



917 



TY fjA-i 



rt l*» s jj~> 



zabwino ndi wochenjeza Otsutsa. 
Koma anthu ambiri sadziwa (Za 
uthenga wako). 

29. Eti akunena: "Nliti 
lidzakwaniritsidwe Lonjezo ili 
(lakudza kwa chiweruziro) Ngati 
mukunenadi zoona? 

30. Nena: "Muli nalo pangano 
(Lotsimikizika) la tsiku (limenelo) 
Limene simungathe kulichedwetsa 
Ngakhale ola limodzi,kapena 
Kulifulumizitsa." 

31. Ndipo amene sadakhulupirire 
akunena: "Sitiikhulupirira Qur'an 
iyi, Ngakhalenso mabuku aja 
apatsogolo Pake. "Ndipo 
ukadawaona achinyengo Pamene 
azikaimiritsidwa pamaso pa 
Mbuye wawo, (ukadaona zoopsa 
Zazikulu), uku pakati pawo 
Akubwezerana mawu. Amene 
Adaponderezedwa adzanena kwa 
amene Adadzikweza: 
"Kukadapanda Inu (Kutipondereza), 
tikadakhala Asilamu." 

32. Amene adadzikweza 
adzanena kwa amene 
Adaponderezedwa: "Ha, kodi ife 
Tidakutsekerezani kuchiongoko 
Chitakudzerani? Iyayi, koma 
mudali Oipa." 

33. Ndipo amene 
adaponderezedwa Adzanena kwa 
amene adadzikweza: "Iyayi, koma 












1 <&Jr**jM{)i 






Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



918 



YY frji-1 



ft L») 5 jj-o 



(mumachita) ndale za usiku Ndi 
usana (zotitsekereza nazo 
Kuchikhulupiriro) pamene 
Mumatilamula kuti tinkanire 
Mulungu Ndikumpangira lye 
milungu inzake". Iwo adzabisa 
madandaulo pamene Adzaona 
chilango. Ndipo tidzaika Magoli 
m'makosi mwa amene 
Sadakhulupirire; kodi angalipidwe 
China, osati zija ankachita. 1 

34. Palibe pamene tidatuma 
mchenjezi M'mudzi uliwonse 
koma opeza bwino Am'mudzimo 
ankanena: "Ndithu, ife Tikuzikana 
zimene mwatumidwa Nazozi." 

35. Ndipo ankanena (monyada): 
"Ife tili Ndi chuma chambiri ndi ana 
(ambiri); Choncho ife sitidzalangidwa 
(pa tsiku la chimaliziro)." 

36. Nena: "Ndithu, Mbuye 
wanga Amamchulukitsira riziki 
(zopatsa) Laulere amene wamfuna 
(ngakhale ali Woipa), ndipo 
amamchepetsera (amene Wamfuna 
ngakhale kuti ndi munthu 
Wabwino). Koma anthu Ambiri 
sazindikira (zimenezi)." 












M'ndime iyi, Mulungu akutifotokozera kuti patsiku la chimaliziro padzakhala 
kukangana pakati pa atsogeleri ndi anthu otsogoleredwa. Izi zidzachitika 
pamene otsogoleredwa adzatsimikiza kuti atsogoleri awo amawasokeza; 
ankangowalangiza zachabe. Potero adzakhala ndi madandaulo aakulu chifukwa 
chotsatira anthu osokera. Komatu madandaulo oterewa sadzawapindulira 
chilichonse popeza mwayi udzakhala utatha kale. Choncho nkofunika kuti 
potsata mtsogoleri aliyense tiyambe taganizira komwe akunka nafe; 
tisangokokedwa ngati nyama pakuti Chauta adatipatsa dalitso lanzeru. 
Choncho tigwiritse ntchito bwino nzeru tsoka lisanatigwere. 



Surat 34. Saba 9 



Juzu 22 



919 I tY,>i 



V £ L-*» 3 j j-» 



37. Ndipo sichuma chanu ndi ana 
anu zomwe Zingakuyandikitseni 
kwa Ife, koma (Chikhulupiriro 
cha) amene Wakhulupirira ndi 
kuchita zabwino. Iwo adzapeza 
malipiro owonjezeka Kwambiri 
pazomwe adachita. Iwo adzakhala 
mwamtendere M'zipinda za ku 
Minda ya Mtendere. 

38. Ndipo amene akuchita 
khama Kulimbana ndi zizindikiro 
Zathu ndi Cholinga choti 
alepheretse (zofuna Zathu,) 
iwowo adzabweretsedwa 
Kuchilango (chamoto). 

39. Nena (iwe Mneneri): 
"Ndithu, Mbuye Wanga 
amamchulukitsira riziki (zaulere) 
Amene wamfuna mwa akapolo 
Ake; Ndiponso amamchepetsera 
(Amene wamfuna). Ndipo 
Chilichonse chimene mupereka, 
lye Adzakupatsani china m'malo 
mwake; lye Ngwabwino popatsa 
zaulere, Kuposa opatsa. 

40. Ndipo (kumbuka iwe 
Mneneri) tsiku limene (Mulungu) 
adzawasonkhanitsa onse ndi 
Kunena kwa angero: "Kodi awa 
Amapembedza inu?" 

41. Adzanena: "Kuyera konse 
nkwanu (Simungakhale limodzi 
ndi milungu ina!) Inu ndinu 
Mtetezi wathu, Osati iwo. Koma 



•• 















%&&X&<£\&£>\& 



2F 



&?&&&&& 



Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



920 



YY *>l 



T t L-*» 5 j j-*> 



amagwadira majini(Ziwanda); 
ambiri mwa iwo (anthu) 
Adakhulupirira izo (ziwanda)". 

42. (Mulungu adzawauza iwo:) 
"Lero Aliyense mwa inu sangathe 
kudzetsa Zabwino ngakhale 
masautso pa ena." Ndipo 
tidzawauza amene adadzichitira 
Okha zoipa: "Lawani chilango 
chamoto Chimene munkachitsutsa". 

43. Ndipo aya zathu zofotokoza 
momveka Zikamawerengedwa 
kwa iwo, amanena, "Sichina uyu 
(Muhammad {SAW}) Koma ndi 
munthu yemwe akufuna 
Kukutsekerezani mapemphero 
amene Amapemphera makolo 
anu."Ndipo Akunena: "Sichina iyi 
(Qur'an) Koma ndibodza 
lopekedwa". Ndipo Amene 
sadakhulupirire akunena Pachoona 
pamene chawadzera: "Sikanthu ichi, 
koma ndi matsenga Woonekera." 

44. Ndipo (ngakhale awa 
Arabu) Sitidawapatse mabuku oti 
aziwawerenga (Buku ili lisanadze); 
ndipo Sitidawatumizirenso 
mchenjezi Patsogolo pako. (Nanga 
akudziwa Bwanji kuti Qur'an iyi 
ndiyonama?) 

45. Ndipo amene adalipo 
iwowo kulibe, Adatsutsa,ndipo 
(awa Arabu) sadapeze Chigawo 
chimodzi m'zigawo khumi 
Zazomwe tidawapatsa iwowo, Koma 



©/ 









L5 






Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



921 "*>' 



V t L— » 5j j-j 



adatsutsa atumiki Anga (Pa zomwe 
adawabweretsera). Nanga chidali 
bwanji Chilango Changa (pa iwo). 

46. Nena: "Ndithu 
ndikukulangizani chinthu 
Chimodzi, kuti muimirire 
chifukwa cha Mulungu; awiriawiri 
ndi Mmodzimmodzi, ndipo kenako 
Mulingalire; (muona kuti uyu 
Muhammad {SAW} chilichonse 
chomwe Akunena nchoona. 
Ndiponso muona Kuti) mnzanuyu 
alibe misala. lye, Sichina, koma 
ndimchenjezi wanu Chisanadze 
chilango chaukali." 

47. Nena: "Chilichonse 
ndakupemphani kukhala Malipiro 
(othandizira kufikitsa uthenga Kwa 
anthu) ndichanu, malipiro anga ali 
kwa Mulungu basi. Ndipo lye Ndi 
Mboni pachilichonse." 

48. Nena: "Ndithu, Mbuye wanga 
Amaponya choonadi (ponseponse 
Kotero kuti chonama chimathawa). 
Ngodziwa (zinthu) zobisika." 

49. Nena: "Choonadi chadza 
(chisilamu); Ndipo chabodza 
(chipembedzo cha mafano) 
Sichidzetsa zachilendo. Ndiponso 
Sichibwerera (kukhala ndi nyonga 
monga Kale)." 

50. Nena: "Ngati ndasokera, 
ndiye kuti Ndadzisokeretsa ndekha 
(ndadziyika Ndekha m'mavuto). 









®&£ 









Surat 34. Saba' 



Juzu 22 



922 



YY *j*-» 



T i L-» 5 j j-» 



Koma ngati Ndaongoka, 
ndichifukwa cha zimene 
Akundivumbulutsira Mbuye 
wanga. Ndithu, lye Ngwakumva; 
ali Pafupi (ndi aliyense)." 

51. Ndipo ukadaona pamene 
Adzanjenjemera (akadzachiona 
Chilango cha Mulungu, adzayesera 
Kuthawa), koma sipadzapezeka 
Pothawira, ndipo adzagwidwa 
Pamtunda wapafupi (asanafike 
kutali). 

52. Ndipo adzanena 
(mophuphaphupha) : 
"Tachikhulupirira (tsopano 
Chipembedzo cha Chisilamu)." 
Koma iwo angaulandire chotani 
Usilamu kumeneko (komwe) 
ndikumalo Akutali, 

53. Pomwe chikhalirenicho 
adachikana Kale Chisilamu. Ndipo 
chobisika Ankachigenda (ndi 
bodza) Kuchokera kumalo akutali, 

54. Ndipo padzatsekeka pakati 
pawo ndi Zimene akuzilakalaka, 
monga momwe Adachitidwira 
anzawo akale. Ndithu, Iwo adali 
m'chikaiko chowakaikitsa 
(Uthenga wa Mulungu). 



®&jf4&*'&\ 












Siirat 35. Fatir Juzu 22 



923 



YY *j*-t To J?\& l^y* 




SURAT FATIR XXXV 

^J£: 




Surayi idavumbulutsidwa ku Makka, Mtumiki Muhammad 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) asadasamuke. Cholinga 
chachikulu cha Surayi ndikulimbikitsa chikhulupiriro mu umodzi 
wa Mulungu ndi kukhoza Kwake ndi kupereka zisonyezo kuti 
lye alipo. Ndi kuthetseratu maziko a kuphatikiza Chauta ndi 
zinthu zina, ndi kulimbikitsa kuti mitima iyeretsedwe ku zoipa, 
ndi kuikometsa ndi makhalidwe abwino. 

Surayi yafotokoza poyamba za Mlengi, amene adalenga 
zolengedwa zonse popanda chofanizira. Adalenga angelo, anthu 
ndi ziwanda. 

Ndipo yapereka zisonyezo ndi maumboni zomwe zisonyeza 
kuti kuuka kwa akufa kudzachitikadi. lye amaukitsa nthaka 
youma pogwetsa mvula kuti imeretse mmera womwe 
umatulutsa zipatso ndi mbewu zosiyana mitundu. lye ndi Amene 
adapanga usiku ndi usana kuti uzisinthanasinthana; kusinthana 
komwe kukusonyeza mphamvu Zake. Ndiponso m'kalengedwe 
ka munthu muli zisonyezo zosonyeza mphamvu Zake pomwe 
adamlenga m'njira zosiyansiyana. 

Surayi yafotokozanso za kusiyana kwakukulu komwe kulipo 
pakati pa okhulupirira ndi osakhulupirira. Ndipo yafanizira 
munthu wosakhulupirira ngati munthu wosapenya; wokhulupirira 
ngati munthu wopenya. 

Yafotokozanso za kukhoza kwa Mulungu pakusiyanitsa 
mitundu ya zipatso ndi zolengedwa zina, monga anthu, nyama 
ndi miyala. Zonsezi zikusonyeza ukulu Wake ndi kukhoza Kwake. 

Surayi yafotokozanso kuti otsatira Muhammad (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) apatsidwa uthenga wolemekezeka woposa 
mauthenga ena onse ochokera kumwamba, powavumbulutsira Buku 
lolemekezeka lomwe mkati mwake muli zonse zimene zimapezeka 
m'Mabuku akale. Ndi kuti omtsatira agawidwa m'magulu atatu: 
(a) Onyozela malamulo (b) abwino (c) achangu pochita zabwino. 

Ndipo Surayi yamaliza ndi kudzudzula opembedza mafano a 
mitengo, miyala ndi zithunzi za anthu. 



Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



924 



YY *jA-l 



fO ^13 9jy> 



Surat Fatir XXXV 



'm-t mm-. 



jit. 



0&£\(£&\&\j 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu (Yekha) Muumbi wa 
thambo ndi nthaka (Popanda 
chofanizira), amene adachita 
Angelo kukhala atumwi eni 
mapiko, Awiriawiri; atatuatatu; ndi 
anayianayi. Amaonjezera 
mkulenga monga momwe Afunira, 
(palibe chimene chihgakanike Kwa 
lye). Ndithu, Mulungu Ngokhoza 
Chilichonse. 1 

2. Chifundo chimene Mulungu 
angatsekule Kwa anthu, palibe 
amene Angachitsekereze. Ndipo 
chimene Angachiletse palibe 
amene Angachipereke kupatula 
lye. Ndipo lye Ndi mwini 
Mphamvu zoposa,Wanzeru Zakuya. 



1 (Ndime 1-2) lye Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse; chimene afuna 
kuti chichitike chimachitika Ndipo palibe chimene chingakanike kulengeka ndi 
lye ngati atafuna kuti chilengeke. Mulungu wadzitamanda m'ndime ziwirizi ndi 
makhalidwe Ake awiri apamwamba. Khalidwe loyamba, ndikukhoza komwe 
ndikusalephera chilichonse chimene wafuna. Khalidwe Lake lachiwiri ndikudalitsa 
madalitso osiyanasiyana pa zolengedwa Zake. Mulungu adalenga thambo ndi 
nthaka popanda chofanizira, natukula thambo kumwamba popanda mzati 
nalikongoletsa ndi nyenyezi. lye ndi Yemwe adayalanso nthaka naika 
mmenemo mmera monga chakudya cha zamoyo, nang'ambamo nyanja ndi 
mitsinje ndi akasupe ndi zina zotero zomwe zikusonyeza mphamvu Zake 
zoposa ndi luso Lake. Ndime yachiwiriyi ikutiphunzitsa kuti chimene Mulungu 
wachipereka kwa munthu monga chuma kukhala ndi moyo wangwiro, kukhala 
ndi nzeru zakuthwa, palibe amene angazitsekereze zimenezi. Ndipo chimene 
Mulungu wam'mana munthu, palibe amene angathe kuchipereka kwa iye. 






©;«& 



Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



925 I H^i 



To ^\3 5jj-»> 



3. E, inu anthu! Kumbukirani 
mtendere Wa Mulungu omwe uli 
pa inu (Pomthokoza). Kodi alipo 
Mlengi wina Osati Mulungu 
amene angakupatseni Riziki 
kuchokera Kumwamba ndi pansi? 
Palibe wina Wopembedzedwa 
mwachoonadi, koma lye. Nanga 
mukutembenuzidwira kuti? 

4. Ndipo ngati angakutsutse 
ndithu, Adatsutsidwanso atumiki 
amene adalipo Patsogolo pako. 
Ndipo zinthu zonse 
Zidzabwezedwa kwa Mulungu. 

5. E, inu anthu! Ndithu, lonjezo 
la Mulungu ndi loona. Choncho 
Usakunyengeni moyo wadziko 
lapansi, Ngakhale mdyerekezi uja 
wamkulu (Iblis), asakunyengeni pa 
za Mulungu. 1 

6. Ndithu, Satana ndi mdani 
wanu; choncho Mchiteni kukhala 
mdani. lye Amaliitanira gulu lake 
kuti likhale gulu La anthu 
akumoto. 2 

7. Amene sadakhulupirire 
(Mulungu ndi Mtumiki Wake), pa 
iwo padzakhala Chilango chaukali; 
koma amene Akhulupirira ndi 


















1 M'ndime iyi Mulungu akutichenjeza kuti tisanyengedwe ndi malangizo a 
Satana akuti: "Chitani mmene mungafunire, Mulungu Wachifundo chambiri 
adzakukhululukirani." 

2 Mulungu watifotokozera kuti satana ndi mdani wathu wakalekale; iye ndi 
amene adatulutsitsa tate wathu Adamu m'Munda wa Mtendere pomulakwitsa. 
Ndipo iye adalumbira kuti adzapitiriza kutisokeretsa. 



Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



926 



11 *>i 



To ^13 5jj-*» 



kumachita zabwino, Iwo adzapeza 
chikhululuko ndi malipiro Aakulu. 

8. Kodi amene zochita zake 
zoipa Zakometsedwa kwa iye 
nkumaziona Kuti nzabwino, 
(ngolingana ndi amene Waongoka 
ndi chiongoko cha Mulungu 
Kotero kuti chabwino nkuchiyesa 
Chabwino; choipa nkuchiyesa 
choipa?) Ndithu, Mulungu 
akumlekerera kuti Asokere yemwe 
wamfuna (Chifukwa chakuti 
safuna kuongoka), Ndipo 
akuongola amene wam'funa. 
Choncho moyo wako usaonongeke 
Chifukwa chowadandaulira iwo. 
Ndithu, Mulungu Ngodziwa Zonse 
zimene (iwo) akuchita. 

9. Ndipo Mulungu ndiamene 
amatumiza Mphepo; choncho 
imagwedeza Mitambo (yamvula) 
ndipo timaifikitsa Kudziko 
lachilala. Ndipo kupyolera 
M'madzi otuluka m'mitamboyo; 
Timaiwukitsa nthaka pambuyo 
pakufa Kwake, (monga momwe 
tikutulutsira Mbewu m' nthaka) 
momwemonso Ndimmene 
kudzakhalira kutuluka Akufa 
(m'manda tsiku la chiweruzo. 

10. Amene akufuna ulemerero, 
(Amvere Mulungu), chifukwa 
Ulemerero wonse ngwa Mulungu. 
Kwa Iye amakwera mawu abwino. 
Ndipo zochita zabwino ndi zimene 












Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



927 



rr >>i 



To ^>li 5jj-*» 



Zimakweza mawu abwinowo. 
Ndipo Amene akuchita ndale 
zoipa, adzapeza Chilango chaukali; 
ndipo ndale zawo Nzotayika, 
(zoonongeka). 

11. Ndipo Mulungu 
adakulengani ndi dothi; Kenako 
ndi dontho la umuna; kenako 
Adakupangani amuna ndi akazi. 
Ndipo Mkazi aliyense satenga 
mimba Ndiponso sabala koma 
kupyolera M'kudziwa Kwake 
(Mulungu). Ndipo Amene 
wapatsidwa moyo, sapatsidwa 
Moyo wautali ndiponso 
sachepetsedwa Moyo wake, koma 
zonsezo zili m'buku (La 
Mulungu) .Ndithu, zimenezo Kwa 
Mulungu nzosavuta. 

12. Ndipo nyanja ziwiri 
(yamadzi ozizira ndi Yamadzi 
amchere) sizili zofanana, Iyi 
yamadzi okoma, ozuna, ndi 
omweka Bwino kamwedwe kake; 
ndi iyi (Ya madzi) amchere 
owawa. Ndipo Kuchokera 
m'zonsezi, mumadya nyama 
Yamatumbi (nsomba zaziwisi). 
Ndipo Mumatulutsa 
zodzikongoletsera (Zimene) 
mumazivala; ndipo m'menemo 
Ukuona zombo zikung'amba 
madzi kuti Mupeze ubwino Wake 
ndi kutinso Inu muthokoze. 












Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



928 



rr tjir\ 



To Jp\& 5jj-*» 



13. Amalowetsa usiku mu 
usana, ndi Kulowetsa usana mu 
usiku; dzuwa ndi Mwezi adazichita 
kuti zigonjere (Malamulo Ake). 
Zonse zikuyenda (Usana ndi usiku) 
kufikira nthawi Yake yodziwika. 
Ameneyo ndi Mulungu, Mbuye 
wanu, Mwini Ufumu. Ndipo 
Amene mukuwapembedza, osati 
lye, Alibe ngakhale khoko la 
chipatso cha Kanjedza. 

14. Ngati mutawapempha 
(mafanowo), Sangamve kuitana 
kwanu, ndipo ngati Atamva 
sangakuyankheni (chifukwa Alibe 
kukhoza kulikonse). Ndipo pa 
Tsiku lomalizira, adzakana 
kuphatikiza Kwanu. Ndipo palibe 
(aliyense) Angakuuze monga 
momwe akukuuzira (Mulungu) 
Wodziwa kwambiri. 

15. E, inu anthu! Inu 
ndiosaukira (chinthu Chilichonse) 
kwa Mulungu; koma Mulungu 
Ngwachikwanekwane (sasaukira 
Chilichonse kwa inu); 
Wotamandidwa (Ndi zolengedwa 
zonse). 

16. Ngati atafuna angakuchotseni 
ndi Kubweretsa Zolengedwa 
zatsopano. 

17. Ndipo zimenezo sizili 
zovuta kwa Mulungu. 












^j^=a4^^I^|<i>l 



©j&y^J*^^ 



Siirat 35. Fatir 



Juzu 22 



929 



Yt *>i 



Y*o ^kis 3j^-» 



18. Ndipo wosenza, sadzasenza 
mtolo wa Wina. (Aliyense 
adzasenza mtolo wa Machimo 
ake). Ngakhale amene Walemedwa 
ndi mtolo wake ataitana (Wina) 
chifukwa cha mtolo wake Kuti 
amsenzere silidzatengedwa 
Ngakhale gawo pang'ono la 
mtolowo (Ndi munthu ameneyo), 
ngakhale Atakhala m'bale wake. 
Ndithu, Ukuchenjeza okhawo 
amene akuopa Mbuye wawo 
pomwe sakumuona, Ndipo 
akupemphera Swala, ndipo 
Yemwe akudziyeretsa, ndithu, 
Akudziyeretsa yekha, (ubwino 
wake Umubwerera iye mwini); 
ndipo Mabwerero (a zolengedwa 
Zonse) ndi kwa Mulungu (basi). 

19. Ndipo wakhungu ndi 
wopenya Ngosafanana, (woyenda 
panjira Ya choona ndi Wosokera 
ngosafanana); 

20. Ngakhale mdima ndi 
kuunika (Nzosafanana); 

21. Ngakhale mthunzi ndi 
kutentha (Nzosafanana); 

22. Ndipo amoyo ndi akufa 
safanana (Amene mitima yawo ili 
ndi moyo Pokhala ndi 
chikhulupiriro, ndi Amene mitima 
yawo ili yakufa Posakhala ndi 
chikhulupiriro, Ngosafanana). 
Ndithu, Mulungu Akumumveretsa 






®&\j{jty\(Sj~^ 



(&2W;«S,Aih5K 



%&\%bw& 









Surat35. Fatir 



Juzu 22 



930 



yy >>i 



To ^kl3 ojj^t 



amene wam'funa; Koma iwe 
sungathe kumumveretsa Amene ali 
m'manda. 

23. Iwe sindiwe chinthu china, 
koma Ndiwe mchenjezi. 

24. Ndithu, Ife takutuma 
mwachoona Kuti unene nkhani 
yabwino (yokalowa Kumunda wa 
Mtendere kwa amene 
Akhulupirira), ndi kuti uchenjeze 
(Za chilango chamoto kwa amene 
Sadakhulupirire). Ndipo palibe 
m'badwo Uliwonse koma 
mchenjezi adapitamo. 

25. Ndipo ngati angakutsutse, 
(sichachilendo). Ndithu, amene 
adali patsogolo pawo Adatsutsanso 
Aneneri awo adawadzera Ndi 
zizindikiro zoonekera poyera, ndi 
Kalata ndi mabuku ounikira (Njira 
yabwino). 

26. Kenako ndidawathira dzanja 
(Ndidawaononga) amene 
adatsutsa. Nanga chidali bwanji 
Chilango Changa (pa iwo). 

27. Kodi sudaone kuti Mulungu 
amatsitsa Madzi kuchokera 
kumitambo? Kupyolera 

m' madzi wo tatulutsa zipatso 
Zautoto wosiyanasiyana (zakuda 
Zofiira, zachikasu, zobiriwira 
pomwe Madzi ake ndiamodzi 
omwewo). Ndipo M'mapiri muli 
timizere: toyera, Ndi tofiira, 






w*££$ £%&* m>38<lij 









Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



931 



rt c>» 



f© jt\3 Sjj-- 



tosiyana utoto wake, Ndi (tina) 
takuda kwambiri. 

28. Ndipo mwa anthu ndi 
nyama zokwawa, Ndi ziweto, 
nchimodzimodzinso; Nzosiyana 
maonekedwe ake (utoto Wake). 
Ndithu odziwa ndi amene 
Amamuopa Mulungu mwa 
akapolo Ake. Ndithu, Mulungu 
Ngwamphamvu Zoposa; 
Ngokhululuka kwambiri. 

29. Ndithu, amene akuwerenga 
Buku la Mulungu uku 
nkumapemphera napereka 
Mzimene tawapatsa mwanseri ndi 
Moonetsera, iwo akuyembekezera 
Malonda osaonongeka, 

30. Kuti akawadzadzire 
malipiro awo ndi Kuwaonjezera 
zabwino Zake; ndithu, lye 
Ngokhululuka kwabasi; 
Ngothokoza Kwambiri. 

31. Ndipo Buku limene 
takuvumbulutsira, Nloona; 
likutsimikizira za mabuku Omwe 
adali patsogolo pake. Ndithu, 
Mulungu kwa akapolo Ake 
Ngodziwa Kwambiri ndiponso 
Akuwaona bwino. 

32. Kenako tidawapatsa Buku 
(Qur'an) Amene tidawasankha 
mwa akapolo Athu, koma alipo 
ena mwa iwo Odzichitira okha 












9 W 9* " 9 ^SS iJ> *9)\ 9>'**jx 



<a 






9>\ 'Z 



^\&K&£lj& 



Surat 35. Fatir 



Juzu 22 932 Y Y *>t 



To ^1?13 Ojj-o 



chinyengo (Pochulukitsa 
machimo), ena mwa iwo 
Nzofanana; ndipo ena mwa iwo 
Ngopikisana pochita zabwino mwa 
Chifuniro cha Mulungu. Kuteroko 
Ndiwo ubwino waukulu. 

33. Adzailowa Minda 
yamuyaya; M'menemo 
adzakongoletsedwa Povekedwa 
zibangiri zagolide ndi ngale; Silika 
ndicho chovala chawo m'menemo. 

34. Ndipo adzanena 
(pakuthokoza kwawo): 
"Kutamandidwa konse nkwa 
Mulungu Amene watichotsera 
madandaulo; Ndithu Mbuye wathu 
Ngokhululuka Kwambiri, 
Ngothokoza kwabasi. 

35. "Yemwe, chifukwa cha 
ubwino Wake, Watikhazika 
m'nyumba yamuyaya; M'menemo 
mavuto satikhudza, Ndiponso 
m'menemo kutopa Sikutikhudza". 

36. Koma amene 
sadakhulupirire, wawo Ndi moto 
wa Jahannama Sikudzaweruzidwa 
kwa iwo kuti afe, Ngakhale 
chilango chake 

Sichidzachepetsedwa pa iwo. Umo 
Ndimmene tikumlipirira aliyense 
wokanira (Mtendere wa Mulungu). 

37. Ndipo m'menemo iwo 
adzakuwa (adzalira uku Akunena): 
"Mbuye wathu! Titulutseni 



&$$ti&2a$k& 












9*99'" i*'. > &' 19 9 ~9} '< 9 9{' 









Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



933 



XT *jJH 



To ^\3 5jj-^ 



(M'moto ndi kutibweza padziko 
Lapansi); tikachita ntchito 
zabwino, Osati zija tinkachita" 
(Mulungu Adzawauza): "Kodi 
sitidakupatseni Moyo wokwanira 
wotheka kukumbuka Kwa 
wokumbuka? Ndiponso Mchenjezi 
Adakudzerani. Choncho lawani 
(Chilango). Ndipo anthu ochita 
zoipa Alibe mpulumutsi." 

38. Ndithu, Mulungu Ngodziwa 
zobisika Zakumwamba ndi za 
pansi. lye Ngodziwa kwambiri Za 
m'zifuwa. 

39. lye ndi Yemwe wakuchitani 
kukhala Osiyirana padziko lapansi 
(akufa Ena, ena nkulowa m'malo 
mwawo). Ndipo amene 
sadakhulupirire, kuipa kwa 
Kusakhulupirirako kuli kwa lye 
mwini. Ndipo kusakhulupirira kwa 
Osakhulupirira sikuwaonjezera 
Chilichonse kwa Mbuye wawo, 
komaNkwiyo basi. Ndiponso 
Kusakhulupirira kwa 
osakhulupirira Sikuwaonjezera 
chilichonse, koma Kutayika basi. 

40. Nena: "Kodi mwawaona 
aphatikizi Anu (awa) amene 
mukuwapembedza M'malo mwa 
Mulungu? Tandionetsani, 
Ndimbali iti yanthaka adalenga; 
Kapena iwo ali ndi gawo 
m'thambo; (Gawo lakulenga 
thambo?) Kapena Tidawapatsa 



& 






<$&<&<&&$# 









Siirat 35. Fatir 



Juzu 22 



934 



yy tji-» 



To ^»13 5jj~* 



Buku (Qur'an iyi Isadadze) kotero 
kuti ali ndi umboni Wapoyera 
wochokera m'menemo 
(Wotsimikizira chipembedzo 
chawo Chamafano?) Koma ochita 
zoipa Salonjezana ena kwa ena 
china chake Koma zachinyengo basi. 

41. Ndithu, Mulungu 
amachirikiza thambo Ndi nthaka 
kuti zisachoke. Ndipo ngati 
Zitachoka, palibe aliyense amene 
Angazigwire kupatula lye. Ndithu, 
lye Ngoleza; Ngokhululuka 
kwabasi. 

42. Ndipo (awa osakhulupirira, 
kale) Adalumbirira Mulungu, 
kulumbira Kwawo kwakukulu, 
kuti ngati Adzawadzera mchenjezi, 
adzakhala Oongoka kuposa 
mbadwo uliwonse. Koma pamene 
mchenjezi adawadzera, Palibe 
chilichonse chidaonjezeka kwa 
Iwo, koma kukana (choonadicho). 

43. Chifukwa cha kudzikweza 
padziko ndi Kuchita chiwembu 
choipa. Ndipo chiwembu Choipa 
sichingamtsikire aliyense koma 
Mwini (yemwe) wachitayo. Kodi 
Akuyembekeza china chosakhala 
Machitidwe (a Mulungu) amene 
Adawapititsa pa anthu akale. 
Koma Supeza kusintha pa 
machitidwe a Mulungu. Ndipo 
supeza kutembenuka pa 
Machitidwe a Mulungu. 









Surat 35. Fatir 



Juzu 22 



935 



YY *>» 



TO ^kl3 5jj-*» 



44. Kodi sadayende padziko 
nkuona Momwe adalili mathero a 
omwe adali Patsogolo pawo? 
Ndipo adali anyonga Kwambiri 
kuposa iwo? Ndipo palibe chinthu 
Chonkanika Mulungu kumwamba 
ndi Pansi. Ndithudi lye Ngodziwa 
Kwabasi Wokhoza. 

45. Ndipo Mulungu 
akadamalanga anthu chifukwa Cha 
zomwe alakwa, sakadasiya 
Pamwamba pake (nthaka) 
chamoyo Chilichonse; koma lye 
amawalekerera Mpaka nthawi 
yomwe adaiikayo. Ndipo nthawi 
yawo ikadzawadzera, (Pompo 
adzalangidwa). Ndithu, Mulungu 
akuwadziwa bwino Akapolo Ake. 



a 







Surat 36. Ya-Sin Juzu 22 I 936 I t X t£\ T*\ Jj 5j^ 




^5 



SURAT YA-SIN XXXVI 



Surayi yayamba ndikutchula malembo awiri omwe amapanga 
mawu m'chiyankhulo cha Chiarabu. Ndipo yatsiriza pazimenezi 
kuilumbirira Qur'an ponenetsa kuti Muhammad (Madalitso ndi 
Mtendere zikhale naye) ndi mmodzi wa atumiki. Ndi kuti iye ali 
panjira yolunjika yomwe yaikidwa ndi Qur'an imene 
yavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mwini mphamvu 
zoposa ndi Wachifundo chambiri, kuti ndi Qur'aniyo achenjeze 
anthu omwe makolo awo akale sadachenjezedwe. 

Surayi ikupereka chithunzi cha otsutsa amene sapindula ndi 
machenjezo. Ndipo ikunenetsa kuti kuchenjeza kumawapindulira 
okhawo omwe ali ndi mitima yochenjezeka ndi yoopa mwini 
chifundo chambiri. 

Yanenanso kuti ndithu, Mulungu adzaukitsa akufa ndi kutinso 
Iye akusunga zochita zonse za akapolo Ake. 

Surayi ikuperekanso fanizo la osakhulupirira a m'Makka 
lomwe likusonyeza poyera mkangano wa pakati pa ovomereza ndi 
otsutsa ndi kunenetsa kwa ndithundithu mapeto a magulu awiriwa. 

Komanso Surayi yakamba za zisonyezo za kukhoza kwa 
Mulungu zomwe zingachititse wanzeru ndi wolingalira 
kukhulupirira ndi kuopa chilango cha Chauta, chomwe chidzadza 
modzidzimutsa pa tsiku lomwe mzimu uliwonse udzalipidwa 
zimene udachita; anthu a ku munda wa mtendere adzasangalala. 
Ndipo adzapeza chilichonse chimene adzachikhumba. Pomwe 
anthu akumoto adzapirikitsidwa ku chifundo cha Mulungu ndi 
kuponyedwa kumoto uku kukamwa kwawo kutatsekedwa, ziwalo 
zawo zikuwaneneza pa zochimwa zawo. 

Ndipo Mulungu akadafuna, akadasintha maonekedwe awo 
pompano padziko lapansi. Iye ndi Yemwe amasintha amene 
moyo wake watalika padziko lino lapansi kukhala nkhalamba 
yopanda mphamvu ndi yochepekedwa nzeru.Ndipo Iye ndi 
Amene adateteza Mneneri wake ku chikhalidwe chamisala ndi 



Surat 36. Ya-Sin Juzu 22 937 Y Y *>i r 1 J4 hf 



kuti sadamphunzitse kulakatula nyimbo zopeka. Ndipo 
sikoyenera kwa iye kukhala mlakatuli wa nyimbo zopeka. 

Surayi ikunenetsanso kuti Mulungu adagonjetsa nyama kuti 
zitumikire anthu ndi kuzikwera. Koma iwo mmalo mothokoza 
Mulungu akupembedza milungu yosakhoza chilichonse. 

Popitiriza Surayi, ikukumbutsa munthu chiyambi cha 
chilengedwe chake ponenetsa kuti chilengedwe chake 
chidachokera kumadzi opanda pake. Koma akakula amakhala 
mwini makani zedi potsutsa zouka ku imfa, chikhalirecho akuona 
zodabwitsa zambiri za Mulungu. 

Mulungu amatulutsa moto mumtengo momwemonso 
mumakhala madzi. Iye adalenga thambo ndi nthaka yochindikala 
ndi yophanuka. Kodi wotere angalephere kubwezera mafupa 
mmalo mwake? 

Iye akaftina chinthu, savutika pakuti chinthucho 
chichitike.Amangoti: "chichitike". Ndipo chimachitikadi. 

Mulungu Ngolemekezeka ndi kupatukana ndi machitidwe 
operewera. Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse. Ndipo kwa Iye 
ndi kobwerera zonse. 




Surat 36. Ya-Sin Juzu 22 938 I Y Y «-j*-i 



Y"l J^ 3j>-» 



£«ra* Fa-Si/t XCm 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. KJ-Sf/i. 

2. Ndikulumbira Qur'an (iyi 
yomwe Yakonzedwa mwaluso) 
yodzazidwa Ndi mawu anzeru. 

3. Ndithu, iwe (Muhammad 
{SAW}) Ndimmodzi wa atumiki 
(amene Mulungu Adawatuma kwa 
anthu kuti Akawasonyeze 
chiongoko). 

4. (Uli) panjira yolunjika. 

5. (Qur'an iyi) nchivumbulutso 
cha Mwini Mphamvu zoposa; 
(palibe chokanika kwa lye) 
Wachisoni, 

6. Kuti uwachenjeze anthu 
omwe atate Awo 
sadachenjezedwe; choncho iwo 
Ngoiwala (zomwe zili zofunika 
Kuchitira Mulungu ndi 
kudzichitira Okha pamodzi ndi 
anthu ena). 

7. Ndithu, mawu (onena za 
chilango) Atsimikizika pa ambiri a 
iwo; Poti iwo sakhulupirira. 

8. Ndithu Ife taika magoli 
m'makosi Mwawo ofika 
kuzibwano, kotero kuti Mitu yawo 



■ t "-■/- ^'~7:m 



0&&\<&&\&\jt. 



ijiT 









#^pc&&&& 









Surat 36. Ya-Sin Juzu 22 



939 



rr *>» 



V% J+> *j>-» 



yayang'anammwamba; (Siingathe 
kutembenuka ndi kuyang'ana). 

9. Ndipo tawaikira 
Chotsekereza patsogolo pawo ndi 
Chotsekereza pambuyo pawo, 
Ndipo maso awo tawaphimba, tero 
Iwo saona (zapatsogolo ndi 
pambuyo Pawo). 

10. Ndipo kwa iwo 
nchimodzimodzi, Uwachenjeze 
ngakhale usawachenjeze 
Sangakhulupirire. 

11. Ndithu, kuchenjeza kwako 
Kupindulira amene watsatira 
Qur'an ndi kumuopa (Mulungu) 
Wachifundo ngakhale sakumuona. 
Wotere muuze nkhani yabwino ya 
Chikhululuko (chochokera kwa 
Mulungu pa machimo Ake) ndi 
malipiro aulemu. 

12. Ndithu, Ife tidzaukitsa 
akufa, Ndipo tikulemba zimene 
atsogoza (M'dziko lapansi 
m'zochita zawo) Ndi zomwe 
amasiya pambuyo (atafa, 
Zonkerankera mtsogolo), ndipo 
Chinthu chilichonse tachilemba 
M'kaundula wopenyeka 
(wofotokoza Chilichonse). 

13. Ndipo atchulire, (iwe 
Mneneri) Nkhani ya eni mudzi 
pamene Atumiki (A Mulungu) 
adaudzera mudziwo (kuti 
Akaongole eni mudziwo). 









' 9? \,7Ci 






fu^irl**y^^<^^ 



<• 9. \ 9 *9<*mU *tb"h9}"&h' 



9 i* 






Surat 36. Ya-Sin Juzu 22 940 Y Y *>» 



Y"1 J*t 5j>-» 



14. Pamene tidatumiza atumiki 
awiri kwa Iwo adawatsutsa; ndipo 
tidawalimbika Iwo (awiriwo) 
potumiza wachitatu. (Atumiki 
atatuwo) adati: "Ife Tatumidwa 
kwa inu." 

15. (Eni mudzi) adati: "Inu ndi 
anthu Ngati ife; (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri 
sadavumbulutse chilichonse (Kwa 
munthu); inu simuli kanthu koma 
Mukunena bodza." 

16. (Atumiki) adati: "Mbuye 
wathu (Amene watituma kwa inu) 
akudziwa Kuti ife ndi otumidwadi 
kwa inu. 

17. Ndipo palibe china pa ife, 
koma Kufikitsa kwachimvekere 
uthenga (Wa Mulungu)." 

18. (Eni mudzi) adati: "Ife 
tapeza Tsoka chifukwa cha inu: 
Ngati Simusiya (ulaliki wanuwo 
wofuna Kutichotsa ku 
chipembedzo chathu) Tikugendani 
ndi miyala; ndipo Kuchokera kwa 
ife chikupezani Chilango chowawa." 

19. (Atumiki) adati: "Tsoka 
lanu Lili ndi inu (chifukwa Cha 
kukana kwanu ndi kupitiriza 
Kupembedza mafano). Kodi 
Mukakumbutsidwa (ndi mawu 
omwe M'kati mwake muli 
mtendere wanu Mukuti 
takudzetserani masoka; ndi 















Siirat 36. Ya-Sin 



Juzu 23 



941 tr*j*-» 



Y"1 J^i 3j>-» 



Kumatiopseza ndi chilango 
chowawa?) Koma inu ndi anthu 
olumpha malire". 

20. Kenako munthu adadza 
akuthamanga Kuchokera 
kumalekezero a mzindawo (Ndipo) 
adati: "E, inu anthu anga! Atsateni 
atumikiwa. 

21. Atsateni omwe 
sakupemphani malipiro 
(Pakukulangizani kwawo), Ndipo 
iwo ngoongoka. 

22. Kodi nchiyani 
chingandiletse ine Kupembedza 
Yemwe adandilenga? Ndipo kwa 
lye ndi komwe inu nonse 
Mudzabwerera. 

23. Kodi ndidzipangire milungu 
Kusiya lye (Mulungu) ? 
Chipulumutso chawo 
Sichingandipindulire chilichonse 
Ngati (Mulungu) Wachifundo 
Chambiri atafuna kundichitira 
Zoipa; Ndipo siingandipulumutse. 

24. Ndithu, ine ngati nditatero 
ndiye kuti Ndili mchisokero 
Choonekera poyera. 

25. Ndithu ine ndakhulupirira 
Mbuye wanu Choncho ndimvereni." 

26. Kudanenedwa (kwa iye): 
"Lowa M'munda wa Mtendere." 
Iye adati: "Ha! Anthu anga, 
Akadadziwa! 












Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 942 TT^i 



*"* Or* 5 JJ~* 



27. Momwe Mbuye wanga 
wandikhululukira Ndikundichita 
kukhala mmodzi wa Opatsidwa 
ulemu (akadakhulupirira)" 

28. Ndipo anthu ake 
sitidawatsitsire ankhondo 
Ochokera kumwamba pambuyo 
pake (Kuti awaononge). Ndipo 
pachizolowezi chathu sititsitsa 
(ankhondo Kumwamba tikafuna 
kuononga, koma Mngelo mmodzi 
amakwanira). 

29. (Kuonongeka kwawo) 
kudali mkuwe Umodzi , ndipo 
nthawi Yomweyo adali akufa (izi 
zidachitika Pamene Jiburil 
adawakuwira Mkuwe 
wamphamvu). 

30. Ha! Nzodandaulitsa kwa 
Anthu! Palibe pamene Mtumiki 
adawadzera popanda Kumchitira 
chipongwe (ndi kukana Kumtsata)! 

31. Kodi sadalingalire za 
mibadwo Yambirimbiri imene 
tidaiononga Patsogolo pawo? 
Ndipo iwo Sangabwererenso kwa 
iwo. 

32. Ndipo zolengedwa zonse 
Zidzaonekera kwa Ife 

33. Ndipo chisonyezo chawo 
Ndi nthaka ya chilala; Timaiukitsa 
(ndi madzi) ndi kutulutsa 
M'menemo njere, Zomwe zina 
mwa izo amadya. 



®^^(^^S®QI^^ 












®t 



S99 9^9 9ft ?9?' 



\&&2 



®&^%f&t$& 






Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 943 YT *>i 



T"V Jh »j>- 






,<"SM '* t'i 9 ' K 9 ' 



rA ^«^(«tej«<a»os> 



34. Ndipo tapanga m'menemo 
minda Ya kanjedza ndi mpesa; 
Ndipo tatulutsa m'menemo 
akasupe. 

35. Kuti azidya zipatso zake 
pomwe Sizidapangidwe ndi manja 
awo. Kodi bwanji sathokoza 
(Mulungu)? 

36. Alemekezeke (Mulungu), 
Amene adalenga zinthu zonse, 
chachimuna ndi Chachikazi, 
kuchokera m'zimene Nthaka 
ikutulutsa, ndi iwo omwe Ndi zina 
zimene (anthu) sakudziwa. 

37. Ndiponso chisonyezo 
chawo Ndiusiku. M'menemo 
timachotsamo Usana (womwe 
umabisa usiku), ndipo (Anthu) 
amangozindikira ali mumdima; 

38. Ndipo dzuwa; limayenda 
m'njira Ndi m'nthawi yake imene 
Idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero 
Chimenecho ncha Wamphamvu 
zoposa, Wodziwa kwambiri. 

39. Ndiponso mwezi; 
tidaukonzera malo Oimirapo 
mpaka kukafika pomwe 
Umabwerera ndi kukhala wochepa 
Ndi wokhota monga nthambi ya 
Mtengo wa kanjedza, youma 
komanso Yokhota. 1 



1 Ndime iyi ikufotokoza za kayendedwe ka mwezi kuti adaupangira malo 28 
oimirapo. Umayamba pamalo woyamba uli wochepa ndi wokhota. Ndipo 
umanka nukula kuchoka pa malo ena nkufika pa malo ena mpaka kukafika 












Surat 36. Ya-Sin 



Juzu 23 



944 I tr^i 



y^ j^ 5 jj-- 



40. Nkosatheka kwa dzuwa 
kukumana ndi Mwezi (njira yake); 
nawonso Usiku sungathe 
kupambana usana (Pakudza nthawi 
yausana isadathe,Koma 
zimasinthana). Ndipo chilichonse 
Mwa izo chimasambira m' njira 
Yake (imene Mulungu 
adachikonzera). 

41. Ndiponso pali chisonyezo 
kwa iwo (Chosonyeza madalitso 
Athu pa Iwo). Ndithu, tidaukweza 
mtundu Wawo mchombo 
chodzazidwa (ndi Zonse zamoyo); 

42. Ndipo tidawapangira 
chonga icho Chomwe 
akuchikwera. ' 

43. Ndipo ngati titafuna tikhoza 
kuwamiza M'madzi, ndipo 
sangapezeke Wowathandiza, 
ndiponso Sangapulumutsidwe. 

44. Koma (sitikuwamiza) 
chifukwa cha Chifundo Chathu pa 
iwo ndi kuti Asangalale kufikira 
nthawi yawo (Yofera). 

45. Ndipo kukanenedwa kwa 
iwo: "Opani zomwe ziri patsogolo 
Panu ndi zomwe ziri Pambuyo 






<$ti^32S*fi36 






@ gM,<&&P®z 






© i^^^^^C^\ 






pomwe umakhala wokwanira mkuwala ndi m'maonekedwe ake. Pamenepa 
mpamalo a 14. Tsono kuchoka apa, umayamba kuchepa pang'onopang'ono 
ndi kubisika mpaka utafika pa malo a 28 pomwe umabisikiratu wonse. 
Kayendedwe ka mwezi ndiko kamazindikiritsa anthu kutha kwa mwezi ndi 
chaka, pomwe kayendedwe ka dzuwa kamazindikiritsa anthu kutha kwa tsiku. 
1 Mulungu ndi Yemwe adapanga zombo ngakhale kuti zidapangidwa ndi 
manja a anthu, chifukwa lye ndi Amene adaphunzitsa anthu kupanga zombozo. 



Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 I 945 I rr *>i 



fl J^ «j>-» 



panukuti muchitiridwe 
Chifundo." (Iwo akunyoza 
Malangizowo). 

46. Ndipo palibe chisonyezo 
chilichonse Mwazisonyezo za 
Mbuye wawo (zosonyeza Umodzi 
Wake ndi kukhoza Kwake) 
Chomwe chidawadzera popanda 
Kuchinyoza ndi kuchikana. 

47. Ndipo kukanenedwa kwa 
iwo: "Patsani (aumphawi) zimene 
Mulungu wakupatsani," 
Osakhulupirira amanena kwa 
Okhulupirira: "Kodi tidyetse 
Yemwe Mulungu akadafuna 
Akadamdyetsa; (titsutsane ndi 
cholinga Cha Mulungu)? Ndithu, 
inu simuli Kanthu koma muli 
m'kusokera Koonekeratu." 

48. Ndipo akunena 
(mwachipongwe kwa 
Okhulupirira): "Kodi lonjezo ili 
(Lakudza kwa chiweruziro), 
Lidzachitika liti, ngati mukunena 
Zoona?" 

49. Palibe chimene 
akuyembekeza, koma Ndi mkuwe 
umodzi womwe Udzawamaliza 
mwadzidzidzi uku iwo 
Akukangana. 

50. Ndipo sangathe kuuza wina 
mawu Pachinthu, ndiponso sangathe 
Kubwerera ku maanja awo. 


















Surat 36. Ya-Sin 



Juzu 23 



946 



tr^i 



?"l Jri s jj~» 



51. Ndipo lipenga lidzaimbidwa 
(loukitsa Akufa); iwo 
adzangozindikira Akutuluka 
m'manda kunka Kwa Mbuye 
wawo uku akuthamanga. 

52. Adzati: "Kalanga ife! Kodi 
Ndani watidzutsa pogona pathu?" 
(Adzawauza) "Izi ndi zimene 
Adalonjeza (Mulungu), 
Wachifundo Chambiri ndi zimene 
adanena Atumiki moona." 

53. Sipadzakhala (china) koma 
mkuwe Umodzi basi; 
adzangozindikira Iwo onse 
atabweretsedwa patsogolo Pathu. 

54. "Ndipo mzimu uliwonse 
lero Suponderezedwa pa 
chilichonse. Ndipo mulipidwa pa 
zokhazo Munkachita." 

55. Ndithu, anthu aku munda 
wa mtendere Lero akhala 
wotanganidwa ndi Chisangalalo. 

56. Iwo ndi akazi awo akhala 
M'mithunzi uku atatsamira 
mipando (Ya mtengo 
wapamwamba;) 

57. M'menemo apeza (mtundu 
Uliwonse) wazipatso ndiponso 
Apeza chilichonse chimene 
Akuchifuna. 

58. "Mtendere (pa iwo)!" 
Limeneli Ndi liwu lochokera kwa 
Mbuye (Wawo), Wachisoni. 















Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 947 Y T *>i 



?^ u~>- 5 J> - 



59. "Ndipo dzipatuleni lero, inu 
oipa! 

60. Kodi sindidakulangizeni, E, 
inu Ana a Adamu kuti 
musapembedze Satana; ndithu, iye 
ndi mdani Woonekera kwa inu. 

61. Ndikuti ndipembedzeni Ine; 
Imeneyi ndi njira yolunjika? 

62. Ndithu, (satana) 
adasokeretsa Anthu ambiri mwa 
inu. Kodi Simumaganizira 
mwanzeru? 

63. Iyi ndi Jahena yomwe 
Mumalonj ezedwa. 

64. Iloweni lero, chifukwa cha 
Kunkana kwanu (Mulungu). 

65. Lero titseka kukamwa 
kwawo. Ndipo manja awo 
atiyankhula Ndipo miyendo yawo 
ichitira Umboni pa zomwe 
amachita." 

66. Ndipo tikadafuna, 
tikadafafaniza maso Awo; ndipo 
akadakhala akuthamangira njira; 
koma Akadapenya chotani? 

67. Ndipo tikadafuna, 
tikadawasintha Kukhala ndi 
maonekedwe a nyama Pamalo 
pawo pomwepo (pamene adali), 
Kotero kuti sakadatha kuyenda 
(Kunka patsogolo) ngakhale 
Kubwerera pambuyo. 












**g&$&£&&i i 









Surat 36. Ya-Sin 



Juzu 23 



948 tr*>» 



^ J^ 5 jj^ 



68. Ndipo amene 
tikumtalikitsira moyo Wake, 
timam'bwezeranso pambuyo 
M'chilengedwe chake (ndi kukhala 
Ngati mwana). Kodi bwanji 
saganizira Mwanzeru? 

69. Ndipo sitidamphunzitse 
(Mtumiki {SAW})Ndakatulo, 
ndipo nkosayenera kwa lye 
(kukhala mlakatuli). Qur'an 
Sichina, koma ndichikumbutso ndi 
Buku lomwe likulongosola 
Chilichonse, 

70. Kuti awachenjeze amene ali 
moyo, Ndi kuti litsimikizike liwu 
(Lachilango) pa osakhulupirira. 

71. Kodi saona kuti Ife 
tawalengera Nyama, m'zimene 
manja Athu akonza, Zomwe iwo 
akuti nzawo, 

72. Ndi kuti tazichita kukhala 
Zowatumikira? Zina mwa izo 
Amazikwerapo; ndipo zina mwa 
Izo amazidya. 

73. Ndipo m'menemo 

(m' nyama) muli Zowathandiza 
(zambiri) ndiponso Zakumwa. 
Nanga Bwanji sathokoza? 

74. Ndipo adzipangira milungu 
(Yabodza) kusiya Mulungu 
(weniweni) Kuti athandizidwe nayo. 

75. (Koma) siingathe 
kuwathandiza; Ndipo iwo (kwa 






X" 






<¥^&&^v%&»M 






@ om$^>>w&%> 



®6i^H^^^^ctf!^£ 



<%^^%&&&$ 



Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 I 949 I rr *> 



^ Jr* *jy* 



milunguyo) ndi Asilikali amene 
akonzedwa Kulondera (mafanowo 
ndi Kuwatumikira). 

76. Mawu awo (onyoza 
Mulungu ndi Okutsutsa iwe) 
asakudandaulitse. Ndithu, Ife 
tikudziwa zimene Akubisa ndi 
zimene akuzionetsera Poyera. 

77. Kodi munthu sazindikira 
kuti Ife Tidamulenga ndi dontho la 
umuna? Koma iye wakhala 
Wotsutsa woonekera. 

78. Ndipo akutiponyera fanizo 
(Lotsutsa kukhoza Kwathu 
kuukitsa Akufa) ndi kuiwala 
chilengedwe Chake (chochokera 
kumadzi opanda Pake). Akunena: 
"Ndani angaukitse Mafupa pomwe 
ali ofumbwa?" 

79. Nena: "Adzawaukitsa 
Yemwe Adawalenga panthawi 
yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa 
kalengedwe ka mtundu Uliwonse. 

80. Yemwe adakupangirani 
moto Kuchokera mumtengo 
wauwisi; Kenako inu mumakoleza 
moto M'menemo. 

81. Kodi Yemwe adalenga 
thambo ndi Nthaka (mukuganiza 
kuti) siwokhoza Kuwalenga (iwo 
kachiwiri) monga Momwe alili? 
Inde! Iye ndiMlengi Wamkulu, 
Wodziwa kwambiri! 



'^mB&®& 



j^psS^MJSi^SSSi 



Zft'lV < 



(££0i&^l&&2% 



© 



(99 s'^"\\' 



v&< 









SI 






<Sx 



Surat 36. Ya-Sin Juzu 23 950 T T *>i 



V"\ Jri «j>- 



82. Ndithu, machitidwe Ake 
akafuna Kuti chinthu chichitike, 
amangonena Kwa icho: "Chitika!" 
Ndipo chimachitika (Nthawi 
yomweyo). 

83. Kotero alemekezeke 
Yemwe m'manja Mwake muli 
ulamuliro pachinthu Chilichonse; 
ndipo kwa lye (ndiko) 
Mudzabwerera nonse." 



e^^SBBss^awefii 



t£$a$& «f^g#$tef52 







Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



951 



rrfrjJH rv oiBUaJi djj- 



PgP" 




SURAT AS-SAFFAT XXXVII W 

J^§ 



Sura iyi yayamba ndi kulumbirira zina mwa zolengedwa za 
Mulungu zomwe zimakhala m'mizere ndi zomwe zimakalipa 
ndi kulakatula kuti Mulungu ndi mmodzi. Ndipo lye ndi Mbuye 
wa thambo ndi nthaka ndi zomwe zili pakati pake Mbuye wa 
kuvuma konse ndi kuzambwe, Yemwe adakongoletsa thambo 
lapafupi ndi dziko lapansi ndi nyenyezi. Ndipo adalichita 
thambolo kukhala lotetezedwa kwa otuluka m'chilamulo cha 
Chauta. 

Surayi, pambuyo ponenetsa za umodzi wa Mulungu, 
yanenetsanso za kuuka ku imfa. Ndipo yaopseza okaika za 
kuukako ponena kuti adzangodzidzimuka akupenya. 

Yalongosolanso zisonyezo zomwe zikusonyeza kutheka 
kwake kwa kuchitika zimenezo. Ndipo iwo akadzaliona tsiku 
limenelo adzanena: "Ha! Hi nditsiku la Malipiro." Ndipo 
kudzanenedwa kwa iwo: "Inde, ili nditsiku la chiweruziro 
lorn we mumalitsutsa." 

Achinyengo adzasonkhanitsidwa pamodzi ndi zimene 
amazipembedza. Ndipo adzayamba kufunsana ndi kukangana 
pakati pawo, uku onse ali mkati mwa Jahena. Ndithu, iwo 
adadzikweza posalabadira umodzi wa Mulungu. Ndipo amatcha 
aneneri awo kuti ngamisala, chikhalirecho adawadzera ndi 
choonadi. Koma okhulupirira adzakhala mumtendere wochuluka 
wa Mulungu. Adzakhalanso akusuzumira ku Jahena kuti aone 
anthu oipa. Ndipo adzawaona ali m'katikati mwa moto. 

Pamenepo iwo adzathokoza Mulungu chifukwa chowapatsa 
chisomo cha kutetezedwa ndi kupulumuka kuzimene amawaitanira, 
zosokera. 

Komanso Surayi ikusimba za malo a osalungama ndi malo a 
olungama. Ndipo yapitiriza kusimba nkhani ya aneneri a 
Mulungu ncholinga chotonthoza Mtumiki Muhammad (SAW) 
pamavuto omwe amapezana nawo. Nkutinso zikhale maphunziro 



Siirat 37. As-Saffat Juzu 23 



952 



TT;>l rV otiUJl 5jj- 



kwa anthu osakhulupirirawo. 

Ndipo Surayi yatsutsa zomwe opembedza mafano ankanena 
kuti ana achikazi nga Chauta, pomwe achimuna ndiwo awo, 
kutinso angelo ndi akazi. Komanso kuti pakati pa lye ndi 
ziwanda pali chibale. 

Mulungu apatukane ndi zimene akusimbazo! Anthu Ake 
ndiwo othangatidwa. Ndipo makamu Ake ankhondo ndiwo 
opambana. 

Ndipo Surayi yamaliza ndi kulemekeza Mulungu ndi 
kumpatula ku zomwe akumufanizira nazo. 




Surat 37. As-Saffat Juzu 23 I 953 rr »>■! rv otsuJi i^ 



SuratAs- Saffat XXXVII 



¥ 



t»j& " >#: 



^ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbira (angelo) 
amene Amandanda m'mizere 
yondondozana, (Popembedza ndi 
kugonjera Mbuye Wawo). 

2. Ndi omwe amaletsa zoipa. 

3. Ndi omwe amalalika ulaliki 
(wa Mulungu ndi kumtamanda 
Mochulukira). 

4. Ndithu, Mulungu wanu 
ndimmodzi Basi. 

5. Mbuye wathambo ndi nthaka, 
ndi Zapakati pake; ndiponso 
Mbuye Wa ku vuma konse. 

6. Ndithu, tidalikongoletsa 
thambo Lapafupi (ndi inu) ndi 
chokongoletsa Cha nyenyezi 
(zowala). 

7. Ndi kuti lisungidwe ku satana 
aliyense Wogalukira (lamulo la 
Mulungu), 

8. Kuti asamvere (zomwe 
zikunenedwa Ndi) zolengedwa 
zolemekezeka (Angelo). Ndipo 
akugendedwa (ndi Kupirikitsidwa) 
mbali zonse, 

9. Kuthamangitsidwa 
mwamphamvu; Ndipo chilango 



q^i^i^u ^v 



9i^(iil)ij 






&$££$&&£ 






H&&&S& 



tjUvfe 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



954 



xr*j*-» rvoiiuiUj^ 



chonkerankera Patsogolo chili pa 
iwo, 

10. Kupatula amene 
wazembetsa mawu (Akumwamba), 
ndipo chikumtsatira lye chenje cha 
moto chowala kwambiri. 

11. Tawafunsa, (otsutsa Zouka 
ku imfa): "Kodi iwo ngovuta 
Kuwalenga kuposa zimene 
tidalenga, (Monga: thambo, 
nthaka, nyenyezi Ndi zina 
zotere)?" Ndithu, iwo Tidawalenga 
kuchokera ku dongo Lonyata, 

12. Koma iwe (Mneneri) 
ukudabwa (za Kutsutsa kwawo 
kuuka ku imfa pomwe Zisonyezo 
zilipo zambirimbiri), Ndipo 
akukuchitira chipongwe (Kudabwa 
kwako). 

13. Ndipo akalalikiridwa, 
salalikirika, 

14. Ndipo akachiona 
chisonyezo (Chosonyeza kukhoza 
kwa Mulungu,) Amachichitira 
chipongwe, 

15. Ndipo osakhulupirira 
amanena "Palibe chilipo apa, koma 
ndi matsenga Woonekera poyera. 

16. Kodi tikadzafa ndi 
kusanduka Fumbi ndi mafupa, 
tidzatulutsidwanso (Kuchokera 
m'mandatili amoyo)? 

17. Pamodzi ndi atate athu akale?" 



*■ 



K^V&2\o&£& 



ao-.v* 






%#>£'. Zffi 









®&m$$ 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



955 



rr s-j*-i rv oi3Ua3i 5jj^ 



18. Nena, (iwe Mneneri): "Inde 
(Mudzaukitsidwa inu pamodzi ndi 
Atate anu) uku inu muli 
onyozeka." 

19. Ndithu, (kuukako) 
ndimkuwe Umodzi 
adzangodzidzimuka Ali moyo, 
akuyang'ana. 

20. Ndipo adzanena (okanawo): 
"Kalangalfe! Kuonongeka 
nkwathu! Hi Nditsiku lija lamalipiro! 

21. (Adzawauza): "Hi nditsiku 
lachiweruzo Lomwe mumalitsutsa 
lija. 

22. (Kudzanenedwa kwa 
angero): "Asonkhanitseni amene 
adali Osalungama pamodzi ndi 
akazi Awo (okana Mulungu) ndi 
milungu Yawo imene 
amaipembedza, 

23. Kusiya Mulungu, ndipo 
asonyezeni Njira ya ku Jahena. 

24. Koma aimikeni pano 
chifukwa iwo Afunsidwa (za 
chikhulupiriro Chawo ndi zochita 
zawo): 

25. "Kodi nchifukwa ninji inu 
(opembedza Mafano) 
simukupulumutsana (monga 
Mumanenera padziko lapansi kuti 
Mudzapulumut sana) ? 

26. Koma iwo adzagonjera Ndi 
kudzipereka (ku lamulo la Mulungu); 



%&#&*# 



^asw^fcKiffi 



a '™»® $s 



*c^fjStoA^K& 









*&®p; 



%&&%$&& 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 I 956 I tr *>i TV oiauaJi Sj^ 



27. Ndipo adzatembenukirana 
ndi Kuyamba kufunsana Ndi 
kudzudzulana. 

28. Ndipo (ofooka) adzanena 
(kwa Odzikweza): "Inu 
mumatidzera Kumbali komwe 
timakuganizira kuti nkwabwino. 
(Ndi kutichotsako Kunka nafe ku 
njira yopotoka). 

29. (Odzikweza) adzayankha: 
"Koma Simudali okhulupirira. 

30. Ndipo tidalibe nyonga 
zokuponderezerani Inu, koma 
mudali anthu opyola Malire (ndi 
kutuluka ku choonadi Cha 
Mulungu). 

31. Choncho mawu a Mbuye 
wathu (Onena za chilango) 
atsimikizika Pa ife; ndithu, ife 
tichilawa (Chilango). 

32. Tidakusokeretsani; nafenso 
tidali Osokera. (Choncho 
musatidzudzule) . " 

33. Ndithu,iwo akathandizana 
chilango tsiku Limenelo (la 
chiweruziro). 

34. Ndithu, (chilango chonga 
chimenecho) Ndimomwe 
timawachitira Olakwira (Mulungu). 

35. Ndithu iwo ankati 
akauzidwa kuti palibe 
Wopembedzedwa mwa choonadi 
koma Mulungu ankadzitukumula 



nsKa#*f«SPB 



m£&&£&si 






®w^OTr^tl?e 






Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



957 tr *>» TV oiduJi 5j^ 



36. Ndipo ankanena: "Kodi ife 
tisiye Kupembedza milungu yathu 
chiftikwa Cha zonena za mlakatuli, 
wopenga?" 

37. Iyayi koma adawadzera ndi 
choonadi (Mthenga wawo 
Muhammad yemwe Siwamisala 
kapena wolakatula Zopeka) ndipo 
adawatsimikizira za Atumiki. 

38. Ndithu, inu (osakhulupirira) 
Mudzalawa chilango chowawa; 

39. Ndipo mudzalipidwa 
zokhazo Zimene mumachita; 

40. Kupatula akapolo a 
Mulungu Oyeretsedwa, 

41. Kwa iwo kuli zopatsidwa 
zodziwika (Ndi Mbuye wawo 
Mulungu), 

42. Zipatso (zamtundu 
uliwonse); Ndipo iwo adzalandira 
ulemu (Waukulu), 

43. M'minda ya mtendere, 

44. Adzakhala pa mabedi (a 
mtengo Wapatali) uku 
akuyang' anizana; 

45. Uku zikuwazungulira zikho 
Zodzazidwa ndi zakumwa 
Zochokera m'kasupe woyenda 
Nthawi zonse, 

46. Woyera, wokoma kwa 
wakumwa (Zakumwazo), 



^8&m&&sk>$& 



>j& 



%&$\<3&i<$\s&. 35 






Siirat 37. As-Saffat Juzu 23 



958 rr *jA-i rv oiiuaJi Sj^ 



47. Mzakumwazo mulibe 
zopweteketsa Mutu kwa ozimwa 
ndiponso iwo Sadzaledzera nazo. 

48. Ndipo kwa iwo kudzakhala 
akazi Ophanuka maso, okongola; 
oyang'ana Iwo okha. 

49. Onga ngati dzira (la 
nthiwatiwa) Losungidwa 
(m'mapiko). 

50. Ndipo adzayang'anizana ndi 
Kuyamba kufunsana (pakati pawo.) 

51. Adzanena wonena mmodzi 
wa iwo:"Ine Ndidali ndimnzanga 
(wopembedza Mafano amene 
amatsutsana Nane za chipembedzo 
ndi Zophunzitsa za Qur'an 
yolemekezeka). 

52. Yemwe amandiuza: "Kodi 
iwe ndiwe Mmodzi wa ovomereza? 

53. Zakuti tikadzafa ndi 
kusanduka Fumbi ndi mafupa, 
(tidzaukanso) Ndi kulandira 
malipiro (pa zochita Zathu)?" 

54. (Wokhulupirira) adzanena 
(kwa Anzake: "Inu anthu a 
kumtendere) Kodi 
simungasuzumire (kumoto kuti 
Nawe umuone mnzako uja)? 

55. Adzayang'ana ndipo 
Adzamuona ali Mkatikati mwa moto. 

56. Adzanena: "Ndikulumbirira 
Mulungu! Udatsala pang'ono kuti 















Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



959 



ir tj*r\ rv oiiu^Ji oj^- 



Undiononge (ndikadakuvomera 
paja Padziko lapansi). 

57. Ndipo pakadapanda 
chisomo cha Mbuye Wanga, 
ndikadakhala mmodzi mwa 
Opezeka ku moto. 

58. Kodi zili choncho kuti 
sitidzafanso (tizingosangalala 
m'munda wa mtendere), 

59. Kupatula imfa yathu 
yoyamba ija, Ndi kutinso ife 
Sitilangidwa?" 

60. Ndithu, izi (zimene 
Mulungu waika M'munda wa 
mtendere) ndiko Kupambana 
kwakukulu. 

61. (Pofuna kupeza) zonga 
zimenezi ogwira Ntchito agwire. 

62. Kodi zimenezo ndilo 
phwando Labwino kapena mtengo 
wa Zaqqum (wowawa kwambiri 
Womwe anthu a kumoto azikadya)? 

63. Ndithu, Ife taupanga 
(mtengo Umenewu) kukhala 
mayeso ndi Chilango cha anthu 
ochimwa (Podzichitira okha 
chinyengo ndi Kupembedza 
mafano.) 

64. Umenewu ndimtengo omwe 
umatuluka Pakatikati pa Jahannama 
(Adaulenga kuchokera kumoto). 

65. Zipatso zake (Nzoipa) ngati 
mitu ya Asatana. 






&(j^ > &&£\ 






e&MmW2§ 






©, 



\$M£ffi6W& 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



960 



tr*j±-i rv oibuoJi ojj- 



66. Ndithu iwo akadya 
mtengowo ndi Kudzaza mimba 
zawo ndi zipatso zake (Pakuti 
sakapeza chakudya china Kupatula 
zipatso za mtengowo). 

67. Komanso, ndithu, kuwawa 
kwa Mtengowo kosakanikirana ndi 
madzi Owira kudzakhala pa iwo. 

68. Kenako ndithu, kobwerera 
kwawo Ndi ku Jahena. 

69. Ndithu, iwo adapeza atate 
awo Ali osokera; 

70. Ndipo iwonso 
adawayendetsa kutsata Mapazi 
awo (mothamanga). 

71. Ndipo, ndithu, akale ambiri 
Adasokera patsogolo pawo; 

72. Ndipo, ndithu, tidatuma 
Achenjezi kwa iwo. 

73. Tapenya momwe adalili 
mapeto a omwe adachenjezedwa. 

74. Kupatula akapolo a 
Mulungu, Oyeretsedwa (iwo 
ndiwo anthu a ku Munda wa 
Mtendere). 

75. Ndithu, Nuhi adatiitana, 
(ndipo Tidamuyankha mayankho 
abwino) Taonani kukhala bwino 
Ife Oyankha. 

76. Ndipo tidampulumutsa iye 
ndi Anthu ake kuvuto lalikulu, 






&v£&3\?fir$tila&3 



^\^mm; 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



961 



yt*jJh rv oialaJi ojj-» 



77. Ndipo tidawachita adzukulu 
ake kukhala Otsala (padziko, oipa 
ataonongeka); 

78. Ndipo tidamsiira mbiri 
yabwino Kwa mibadwo yodza 
pambuyo pake. 

79. Mtendere ukhale pa Nuhi pa 
zolengedwa Zonse. 

80. Ndithu, umu ndimomwe Ife 
tilipirira Ochita zabwino. 

81. Ndithu iye ndi mmodzi 
mwa akapolo Athu Amene 
adatikhulupirira. 

82. Kenako tidawamiza enawo. 

83. Ndipo ndithu, Ibrahim adali 
m'gulu Lake; (adayenda 
mayendedwe ake). 

84. Kumbuka pamene adadza 
kwa Mbuye Wake ndi mtima 
woyera, (wogonjera Malamulo). 

85. Pomwe adanena kwa bambo 
wake ndi Anthu ake: 
"Mukupembedza chiyani? 

86. Ha! milungu yopeka Kusiya 
Mulungu, Ndi imene mukuifuna? 

87. Kodi maganizo anu ngotani 
pa Mbuye Wazolengedwa zonse?" 

88. Ndipo adayang'ana 
nyenyezi mozama. 

89. Ndipo adanena: "Ine ndine 
wodwala!" 









9 flfi U X &KX'Z 



^dPS^ 



efe^js 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



962 



vr tj*r\ rvoiduiiSj^ 



90. Choncho iwo adatembenuka 
ndi kumsiya. 

91. (Ibrahim) adapita mozemba 
kumafano Awo, ndipo adawauza 
(mwachipongwe:) "Bwanji 
simukudya (chakudya chomwe 
Chaikidwa patsogolo panupo)? 

92. Bwanji simukuyankhula?" 

93. Atatero adawatembenukira 
ndi Kuwamenya (mwamphamvu) 
ndi dzanja Lamanja. 

94. (Pamene adamva eni 
mafanowo) Adadza kwa iye 
akuthamanga. 

95. Anati: "Kodi mukupembedza 
(miyala) Imene mwasema? 

96. Chikhalirecho Mulungu 
ndiye Adakulengani ndi zimene 
mukuchita!" 

97. (Iwo) adati: "Mmangireni 
ng'anjo, Ndipo mponyeni 
m'motowo." 

98. Adafuna kumchita chiwembu 
(kuti amuphe ndi moto), koma 
tidawachita Kukhala onyozeka. 

99. Ndipo (Ibrahim) adati: 
"Ndithu ine Ndikupita kwa Mbuye 
wanga Iye andiongolera. 

100. O, Mbuye wanga! 
Ndipatseni mwana Yemwe 
adzakhale (mmodzi) mwa 
Olungama!" 












Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



963 



tr*>i rvoiiuJioj^ 



101. Ndipo tidamuuza nkhani 
yabwino Ya mwana wofatsa, 
(Mwanayo ndi Ismaila). 

102. Ndipo (adabadwa ndi 
kuyamba kukula.) Pamene 
adakwana msinkhu Woyenda 
pamodzi ndi tate wake 
Pochitachita za m'dziko (Ibrahim 
Adayesedwa mayeso kupyolera 
M'maloto omwe adalota). Adati: 
"E, mwana wanga! Ine Kutulo 
ndikuona maloto (oona Ochokera 
kwa Mulungu omwe 
Akundilamula) kuti ndikuzinge 
(Monga nsembe yopereka Kwa 
Mulungu). Nanga ukuti Bwanji?" 
(Mwana wabwino) adanena: 
"Bambo wanga! Kwaniritsani 
chimene Mukulamulidwa. Ngati 
Mulungu Afuna, mundipeza ndili 
mmodzi Mwa opirira." 

103. Pamene adagonjera onse 
awiri (chofuna Cha Mulungu), 
ndipo (Ibrahim) Adam'goneka 
chakumphumi (Ndipo adatsimikiza 
kumupha). 

104. Ndipo tidamuitana: "E, 
iwe Ibrahim. 

105. Ndithu, wavomereza 
maloto! (Choncho usamuphe 
mwana wakoyo)." Umo ndi momwe 
timawalipirira Ochita zabwino. 

106. Ndithu,amenewa 
Ndimayeso oonekera, 






Q$03Cp[& 



fys&3& 






e^3S3tfto& 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 964 tr *&\ TV oiauJi Sjj- 



107. Ndipo tidampulumutsa 
pompatsa nyama Yayikulu (yoti 
apereke nsembe.) 

108. Ndipo tidamsiira (mbiri 
yabwino) Kwa anthu ena (amene 
adadza Pambuyo pake). 

109. Mtendere ukhale pa 
Ibrahim! 

110. M'menemo ndi momwe 
timawalipirira Ochita zabwino. 

111. Ndithu, iye adali mmodzi 
mwa Akapolo Athu okhulupirira. 

112. Ndiponso tidamuuza 
nkhani yabwino (Yoti akhala ndi 
mwana wotchedwa) Isihaqa; 
mneneri; wam'gulu la Olungama. 

113. Ndipo tidamdalitsa iye ndi 
(mwana wake) Isihaqa; ndipo 
m'mbumba ya awiriwa 
Mudapezeka abwino ndi 
odzichitira Zoipa owonekera. 

114. Ndipo ndithu, 
tidawachitira zabwino Musa ndi 
Haruna, (powapatsa uneneri ndi 
Madalitso ambiri). 

115. Ndipo tidawapulumutsa 
(awiriwa) Ndi anthu awo Ku vuto 
lalikulu; 

116. Ndipo tidawathangata 
(powagonjetsera Adani awo), 
ndipo iwo adali opambana. 






4gtfid#G$ 















&&tetj&$&'j& 



®j^&\<3^&ffi$& 



&0$'M!&&jZ> 



Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



965 



Yr*jJi-l TV OlSUflJl «j^- 



117. Ndipo tidawapatsa (Musa 
ndi Haruna) Buku losonyeza 
poyera (malamulo;) 

118. Ndipo tidawaongolera ku 
njira Yolunjika. 

119. Ndiponso tidawasiira 
(mbiri Yabwino) kwa anthu ena 
(amene Adadza pambuyo pawo). 

120. Mtendere ukhale pa Musa 
ndi Haruna! 

121. Ndithu umu ndi momwe 
Ife Timawalipirira ochita zabwino. 

122. Ndithu, awiriwa adali 
m'gulu la Akapolo Athu 
okhulupirira. 

123. Ndipo ndithu, Iliyasa ndi 
mmodzi wa Otumidwa. 

124. (Kumbuka) pamene 
adanena kwa anthu Ake:"Bwanji 
Simuopa (Mulungu)? 

125. Mukupembedza (fano 
lotchedwa) Baala ndi kusiya 
(kupembedza) Yemwe adalenga 
zolengedwa M'kalengedwe 
kabwino, 

126. Mulungu, Mbuye Wanu 
ndi Mbuye wa Atate anu akale?" 

127. Koma adamtsutsa; ndithu, 
iwo Adzaonekera (kumoto), 

128. Kupatula akapolo a 
Mulungu amene Ayeretsedwa (ndi 
Mulungu). 






©, 



«"?. *J\i\i f * \' f *\ 









Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



966 



rr*>i rv oi3Ua)i 5jj- 



129. Ndipo tidamsiira (mbiri 
yabwino) Kwa anthu ena (amene 
adadza Pambuyo pake). 

130. Mtendere ukhale pa Uiyasa! 

131. Ndithu umo ndi mmene Ife 
timawalipirira Ochita zabwino. 

132. Ndithu, iye adali mmodzi 
mwa Akapolo Athu okhulupirira. 

133. Ndithu, Luti ndi mmodzi 
wa otumidwa. 

134. (Kumbuka) pamene 
tidampulumutsa Iye ndi anthu ake 
onse, 

135. Kupatula nkhalamba 
yachikazi; Idali mwa otsalira. 

136. Kenako tidawaononga 
enawo (omwe Adali oipa). 

137. Ndithu, inu ( amzinda 
wa Makka) Mumadutsa pa malo 
pawopo m'mawa, 

138. Ndi usiku. Kodi bwanji 
simuzindikira? 

139. Ndithu, Yunusu ndi 
mmodzi wa otumidwa. 

140. (Kumbuka) pamene 
adathawira Mchombo 
chodzazidwa (ndi katundu), 

141. Choncho adachita mayere, 
ndipo adali M'gulu la omgwera 
(mayerewo). 



®&rM*&& 



ifj 






®0#d6&& 



•#RSJ# 






Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



967 



rr*>i rv oidUflii oj^ 



142. Choncho nsomba 
Idammeza uku ali 
Wodzudzulidwa. 

143. Kukadapanda kuti iye adali 
m'modzi Mwa otamanda ndi 
kulemekeza Mulungu, 

144. Akadakhala mmimba 
mwake Mpaka tsiku loukitsidwa 
Zolengedwa ku imfa). 

145. Koma tidamponya Pa 
gombe uku ali Wodwala, 

146. Ndipo tidammeretsera 
mmera wa ntundu Wa mankhaka. 

147. Ndipo (atachira) 
tidamtuma ku anthu Okwana zikwi 
zana limodzi (100,000) Kapena 
kupambana apa. 

148. Ndipo adakhulupirira (ndi 
kuvomereza Ulaliki wake); 
choncho tidawapatsa Chisangalalo 
kufikira nthawi (ya Imfa yawo). 

149. Choncho afunse: "Kodi 
Mbuye Wako ndiye woyenera ana 
Achikazi, ndipo iwo, Achimuna? 
(Pomwe iwo Akabereka mwana 
wachikazi Amanyansidwa naye)"! 

150. Kapena kuti tidalenga 
Angelo kukhala Akazi, iwo akuona? 

151. Chenjera ndi bodza 
lawolo; ndithu, Iwo akunena: 

152. "Mulungu wabereka." 
Ndithu, iwo ndi Abodza. 









Siirat 37. As-Saffat Juzu 23 



968 



tr^i rv oi3UaJUjj-- 



153. Kodi lye adasankha ana 
achikazi kusiya Achimuna? 

154. Kodi nchiyani chakupezani 
(kuti Muweruze mopanda 
chilungamo); Nanga mukuweruza 
bwanji (zimenezi)? 

155. Kodi bwanji 
simukumbukira, (Mwaiwala 
zisonyezo zake zodabwitsa Ndi 
kupatukana kwake ndi zimenezo)? 

156. Kapena inu muli ndi 
umboni Woonekera (wochokera 
kumwamba)? 

157. Tabweretsani buku lanulo 
(momwe Mwalembedwa zimenezi) 
ngati Mukunena zoona. 

158. Ndipo adapeka chibale 
pakati pa lye (Mulungu) ndi 
ziwanda; (pomwe Ziwanda 
nzobisika kwa iwo). Ndithu, 
Ziwanda zimadziwa kuti iwo 
Osakhulupirira akaonekera (kwa 
Mulungu kuti aweruzidwe)! 

159. Walemekezeka Mulungu! 
Ndi Kupatukana ndi zimene 
Akumnamizira! 

160. Koma akapolo a Mulungu 
oyeretsedwa, (Ali kutali ndi 
zimene akusimba 
Osakhulupirirazi). 

161. Ndithu, inu osakhulpirira 
ndi zimene Mukuzipembedza 
(kusiya Mulungu), 









Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



969 tr^i rv oiduoji Sj^- 



162. Ndi zimenezo 
Simungamsokeretse aliyense. 

163. Kupatula yemwe 
(Mulungu adadziwa Kuti) ngolowa 
ku Jahena. 

164. Ndipo (Angelo adanena): 
"Aliyense mwa ife ali ndi malo ake 
Odziwika; 

165. Ndipo ena mwa ife 
ngondanda M'mizere (ya 
mapemphero nthawi Zonse); 

166. Ndipo ena mwa ife 
ngolemekeza (Mulungu nthawi 
zonse ndi Kumtamanda ndi 
kumpatula ku zinthu Zosayenerana 
ndi ulemerero wake)." 

167. Ndipo (osakhulupirira) 
ankati: 

168. "Tikadakhala ndi Buku 
monga lomwe Anthu akale adali 
nalo, 

169. Tikadakhala akapolo a 
Mulungu, Oyeretsedwa." 

170. Koma (pamene 
lidawadzera Bukulo), Adalikana; 
choncho posachedwa Adziwa 
(zotsatira zake). 

171. Ndipo ndithu, liwu lathu 
lidatsogola kwa Akapolo athu 
Otumidwa, 

172. (Kuti) ndithu iwo 
ngopulumutsidwa. 






** 






\&m 






Surat 37. As-Saffat Juzu 23 



970 



rr*j*-» rvotfuiisj^- 



173. Ndipo ndithu, asilikali 
Athu ndi opambana. 

174. Choncho, asiye kwa 
Kanthawi kochepa, 

175. Ndipo ingowayang'ana 
basi; Posachedwapa aona! 

176. Kodi chilango chathu 
Akuchifulumizitsa? 

177. Choncho chikadzatsika 
pabwalo lawo, Udzakhala mmawa 
woipa kwa Ochenjezedwa! 

178. Ndipo asiye kwa Kanthawi 
kochepa, 

179. Ndipo ingowayang'ana 
basi; Posachedwapa aona. 

180. Mbuye wako, Mwini 
Ulemerero, Wapatukana ndi 
Zimene akumnamizira 
(Osakhulupirira). 

181. Ndipo mtendere ukhale pa 
atumiki Onse. 

182. Ndipo kuyamikidwa konse 
nkwa Mulungu, Mbuye wa 
zolengedwa Zonse. 






:~ &S8L*& 













Surat 38. Sad Juzu 23 



971 



TT *j£-l FA Jfi 5jj-* 




Surayi ikupereka chinthunzi kwa ife cha makani a anthu 
opembedza mafano pakutsutsa ulaliki wa Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye), ndi dumbo pokwiya ndi madalitso amene 
Mulungu adampatsa pomuninkha uneneri ndi kumvumbulutsira 
Qur'an. Ndipo yawayankha pamaganizo awo achabe. 

Ndipo yafotokoza kuti chimene chawachititsa iwo kulimbana 
ndi uthenga wa Mtumiki(SAW), ndikudzitukumula basi ndi 
kukonda makani. Ndipo yafotokozanso kuti chikadawatsikira 
chilango cha Chauta sibwenzi akumunenera Mtumiki wa 
Mulungu zomwe akunenazo. 

Mulungu waperekanso mafanizo a anthu akale omkana ndi 
kuonongeka kwawo kuti mafanizo amene wa akhale machenjezo 
kwa iwo, ndi kuti asiye makani. Ndipo chinanso ndi 
kumulimbikitsa Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye), kupirira ngakhale akumane ndi zovuta zotani 
kuchokera kwa anthu opembedza mafano. Ndi kutinso 
azithokoza Mulungu pa mtendere umene wampatsa, monga 
momwe amachitira anzake, aneneri ndi atumiki. 

Komanso Surayi yatchula zimene Mulungu wakonzera anthu 
oopa lye, omwe ndimabwerero abwino. Ndi zimene 
wawakonzera anthu opyola malire, omwe ndimabwerero oipa. 

Kenako yawakumbutsa zimene zidachitika pakati pa tate 
wawo Adamu, ndi Iblis, kuti adziwe kuti kudzikweza posiya 
kutsatira choona, ndi machitidwe ausatana. Ndi kuti adziwenso 
kuti kudzikweza nkomwe kudampirikitsitsa Iblis kuchokera 
kuchifundo cha Mulungu. 

Ndipo Surayi yathera pofotokoza ntchito ya Mtumiki yomwe 
ndikufikitsa uthenga kwa anthu, ndi kuti iye sapempha malipiro 
pantchitoyi kuchokera kwa anthu. Ndiponso kuti ntchitoyi 
sadampatse anthu koma Chauta ndiye adamtuma. Ndipo Qur'an 
ndichikumbutso kwa zolengedwa zonse. Ndipo adzadziwa 
kunena zoona kwa aneneri a Mulungu patapita nthawi. 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



972 



rr tjA-i 



t"A JS ijy* 



Surat Sad XXXVIII 



s^nw^sfefcor; 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Sad; Ndikulumbira Qur'an 
(iyi) ya ulaliki (Wothandiza). 

2. Koma amene 
sadakhulupirire Akudzitukumula 
ndi makani. 

3. Kodi ndimibadwo ingati 
taiononga Patsogolo pawo? 
Adakuwa kuitana (Panthawi 
imeneyo), koma nthawi 
Yopulumuka idali hatha. 

4. Ndipo anadabwa atawadzera 
Mchenjezi wochokera mwa 

i wo. Ndipo Osakhulupirira adati: 
"Uyu ndiwamatsenga; Ngwabodza 
lamkunkhuniza! 

5. Ha! Waichita milungu 
yambirimbiri Ija kuti ikhale 
Mulungu mmodzi Yekha? Ndithu, 
ichi nchinthu Chodabwitsa." 

6. Ndipo adanyamuka 
akuluakulu a mwa I wo nati: 
Nyamukani Muzikapitiriza 
kupembedza Milungu yanu. 
Ndithu, chinthu Ichi (nchoipa); 
chikulinga ife (Kuti tisiyane ndi 
milungu yathu). 

7. "Sitidamve zimenezi (zakuti 
Mulungu Ndimmodzi ngakhale) 



o^l^l^W- 



-^ 















fo$lW&toW&fr 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



973 



TT *jk\ 



TA Jfi 5jj^* 



m'chipembedzo Chakale 
(chikhrisitu) ichi sikanthu, koma 
Ndibodza lopeka." 

8. "Kodi uthengawo (wakuti 
Mulungu Ndimmodzi) 
wavumbulutsidwa kwa iye Pakati 
pathu?" Koma iwo Akukaika ndi 
ulaliki Wanga. Koma Sadalawebe 
chilango Changa. 

9. Kodi iwo ali nazo nkhokwe 
Za chifundo cha Mbuye wako, 
Wamphamvu zoposa, wopatsa 
Mochuluka? 

10. Kapena ufumu wa 
Kumwamba ndi pansi ndi zapakati 
Pake, ngwawo. Ngati zili choncho 
Atakwera makwerero (kuti akafike 
Pamalo poti akalamulire zimene 
Akufuna, ngati angathe kutero). 

11. Awa (Akuraishi) kuonjezera 
pa Kudzitama kwawo, nkagulu 
kochepa Ndi kofooka. 
Kagonjetsedwa monga Makamu 
ankhondo (omwe Adagonjetsedwa 
kale omwe amatsutsana Ndi 
aneneri akale).. 

12. Patsogolo pawo, anthu a 
Nuhi, Adi Ndi Farawo, mwini 
nyumba zitalizitali (Pyramid), 
adatsutsa (aneneri awo) 

13. Ndi Asamudu, ndi anthu a 
Luti ndi (Anthu a Shuaibu) eni 
mitengo Yambiri yothothana, 
makamu amenewa. 









^ISi^JS 2 *^ 









Surat 38. Sad 



Juzu 23 



974 I tr^>» 



TA Jfi 5jj-» 



14. Onsewa adatsutsa atumiki; 
basi Chilango changa 
chidatsimikizika (Pa iwo). 

15. Ndipo awa (Akuraishi), 
sayembekeza China koma mkuwe 
umodzi Wosabwereza.(Ndipo 
ukadzachitika, Onse adzafa). 

16. Ndipo akunena 
(mwachipongwe): "O, Mbuye 
wathu! Tipatsirenitu gawo La 
chilango chathu lisanafike tsiku 
Lachi werengero . " 

17. Pirira (iwe Mtumiki) ku 
zimene Akunenazo (kwa iwe), 
ndipo kumbuka Kapolo wathu 
Daudi, wamphamvu (pa 
Chipembedzo ndi zam'dziko 
lapansi). Ndithu lye 
ngotembenukira kwa Mulungu 
Kwambiri. 

18. Ndithu, Ife tidawagonjetsa 
mapiri kuti Pamodzi ndi iye 
Alemekeze (Mulungu) M'mawa 
ndi madzulo. 

19. Ndi mbalame zomwe 
Zidasonkhanitsidwa Zonse 
zimam vera iye. 

20. Ndipo tidaulimbikitsa 
ufumu wake ndi Kumpatsa uneneri 
ndi kuyankhula Kwa luntha 
(kosiyanitsira choonaNdi chonama). 

21. Kodi yakufika nkhani ya 
okangana Pamene adakwera 



M%33<j3nc$*#a 



^o*u^*ajijBo 



©< 



&&&&P%1$& 



®^WU2 






C$£l^}Z.dc%\%0&\ 



k;\Ms 






Surat 38. Sad 



Juzu 23 



975 tr,>i 



VA jp l)$*> 



chipupa mpaka Kuchipinda (cha 
Daudi Chochitira mapemphero)? 

22. Pamene adamulowera 
Daudi, adachita Nawo mantha 
adati: "Usaope; (Ife) ndife 
okangana awiri, mmodzi Wathu 
wamchenjerera wina. Weruza 
Pakati pathu mwachilungamo, 
Usakondere, ndipo tisonyeze njira 
Yoongoka." 

23. "Ndithu, uyu m'bale wanga 
ali ndi Nkhosa makumi asanu ndi 
anayi Mphambu zisanu ndi zinayi 
(99), ine Ndili ndi imodzi; Ndipo 
akuti: "Ndipatse nkhosa Imodziyo 
kuti ndizikusungira; ndipo 
Wandiposa pakuyankhula. 

24. (Daudi) adati: "Zoona, 
wakuchitira Zosalungama 
pokupempha nkhosa yako Imodzi 
kuti aiphatikize ndi nkhosa zake. 
Ndithu, ambiri mwa ophatikidzana 
nawo Zinthu, ena amachenjerera 
ena kupatula Amene akhulupirira 
ndi kumachita Zabwino; ndipo iwo 
ngochepa." Basi Pamenepo Daudi 
adaona kuti Tamuyesa mayeso 
(ndipo Sadapambane). Choncho 
Adapempha chikhululuko kwa 
Mbuye Wake; adagwa ndi 
kulambira ndi Kubwerera kwa 
Mbuye wake. 

25. Choncho tidamkhululukira 
iye Zimenezo; ndithu, iye ali nawo 












< p&ub'4®&&0&2 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



976 



IT tj*r\ 



VA Jfi 5j^-» 



Ulemerero kwa Ife ndi mabwerero 
Abwino. 

26. "E, iwe Daudi! Ife takuchita 
iwe Kukhala woyang'anira 
padziko; Choncho weruza pakati 
pa anthuwa Mwachilungamo; 
ndipo usatsatire Zilakolako kuopa 
kuti zingakusokeretse Ku njira ya 
Mulungu." Ndithu, Amene 
akusokera ku njira ya Mulungu 
(Potsatira zilakolako zawo), 
chilango Chaukali chili pa iwo 
chifukwa cha Kuiwala kwawo 
tsiku lachiwerengero. 

27. Ndipo sitidalenge thambo 
ndi nthaka ndi Zapakati pake 
popanda cholinga. Zoterezo ndi 
maganizo a amene 
Sadakhulupirire. Choncho 
Kuonongeka kwakukulu ku moto 
Kuli kwa iwo amene 
sadakhulupirire. 

28. Kodi tingawachite amene 
Akhulupirira (Mulungu) ndi 
Kuchita zabwino kukhala monga 
Oononga padziko? Kapena 
tiwachite Oopa (Mulungu) monga 
oipa? 

29. (Hi), ndibuku lochuluka 
madalitso lomwe Talivumbulutsa 
kwa iwe kuti (anthu) Azame 
kwambiri pomvetsetsa ndime 
Zake; ndi kuti apeze nalo phunziro 
eni Nzeru. 















Siirat 38. Sad 



Juzu 23 



977 



yr tjk-\ 



VA Jp S^j-* 



30. Ndipo Daudi tidampatsa 
(dalitso Lobereka) Sulaiman, 
amene adali Munthu wabwino. 
Ndithu, iye adali Wochulukitsa 
kutembenukira kwa Mulungu (ndi 
kuzichepetsa M'chikhalidwe chake 
chonse). 

31. (Kumbuka) pamene 
adasonyezedwa Kwa iye m'nthawi 
yamadzulo Akavalo ofatsa akaima; 
othamanga Kwambiri, akayenda. 

32. Ndipo adati: "Ndikukonda 
zinthu Zabwino chifukwa 
chokumbukira Mbuye wanga," 
Kufikira pomwe (Akavalowo) 
adabisika kuseri kwa Chotsekereza 
(poikidwa m'makola Mwawo 
pomwe iye amafunitsitsa 
Kumawaonabe). 

33. (Ndipo adati): "Abwezeni 
kwaine." Kenako adayamba 
kuwasisita M'miyendo ndi 
m'makosi (Mwawo). 

34. Ndithu, Sulaiman 
tidamuyesa (mayeso); Ndipo 
tidaika thupi pampando wake; 
Kenako adabwerera Kwa 
Mulungu. 

35. Adati: "O, Mbuye wanga! 
Ndikhulukireni Ndipo ndipatseni 
ufiimu (umene) Sangaupeze 
aliyense pambuyo panga; Ndithu, 
inu ndiwopatsa Mochulukitsa." 



^W^X^gSW^ 









iy^\^(3jfiS«SS 









Surat 38. Sad 



Juzu 23 



978 



rr tji-i 



TA Jp 5j^*» 



36. Kenako tidaichita mphepo 
yoomba Moleza kuti imgonjere, 
yomwe Imayenda mwachifuniro 
chake (Sulaimani), paliponse 
pomwe Wafuna, 

37. Ndiponso (tidamgonjetsera) 
asatana; Ena mwa iwo omanga 
zomangamanga Ndi obira 
m'nyanja zakuya, 

38. Ndi ena (mwa asatana) 
onjatidwa Mmagoli ndi unyolo, 
(Kuti asiye kusokoneza ena). 

39. (Ndipo adauzidwa iye): "Izi 
(zomwe takudalitsa nazo) ndi 
Zopatsa Zathu; choncho mpatse 
kapena Mmane (amene wamfuna). 
Popanda Kuwerengeredwa. 

40. Ndithu, (Sulaiman) ali nawo 
Ulemerero waukulu woyandikira 
kwa Ife, ndi mabwerero abwino. 

41. Kumbuka, (iwe Mtumiki 
{SAW}!) kapolo Wathu Ayubu, 
pamene adaitana Mbuye Wake: 
"Ine wandikhudza satana Ndi 
masautso ndi zowawa!" 

42. (Tidamuyankha kuitana 
kwake, Ndipo tidamuuza): 
"Menyetsa miyendo Yako 
(panthaka; patuluka madzi) Ozizira 
osamba ndi kumwa (Zikuchokera 
zomwe uli nazo)." 

43. Ndipo tidamubwezera anthu 
ake, Ndi kumpatsanso ena onga 






a 



'\j&&8®& 









•d, ' 












Surat 38. Sad 



Juzu 23 



979 



tr *jk-\ 



fA Jfi 5jj~» 



vmhs\ 



1^ .v.* 






iwo (M'kuchuluka kwawo) 
powaphatikiza ndi Omwe adali 
nawo; (tidachita zimenezi) 
Chifukwa cha chifundo chochokera 
Kwa Ife ndi kuti chikhale 
chikumbutso Kwa eni nzeru. 

44. "Ndipo gwira m'dzanja lako 
mtolo Wa zikoti; menya ndi 
mtolowo Ndipo usaswe lonjezo." 
Ndithu, Ife Tidampeza ali wopirira. 
Taonani kukhala Bwino munthu! 
Ndithu lye Ngotembenukira 
kwambiri kwa Mulungu. 1 

45. Kumbukira, (iwe 
Mtumiki{SAW}) akapolo Athu 
Ibrahima, Isihaka ndi Yakubu, Eni 
mphamvu (pa ntchito 
yachipembedzo) Ndi kuyang'ana 
kozindikira. 

46. Ndithu, Ife tidawasankha 
powapatsa Chikhalidwe chabwino 
(chomwe) ndi Kukumbukira 
nyumba yomaliza (Nthawi zonse). 

47. Ndithu, kwa Ife iwo adali 
mwa anthu Abwino omwe 
Adasankhidwa. 

48. Ndipo kumbuka Ismail, 
Aliyasa, ndi Dzulikifili; ndipo onse 
iwo adali mwa Abwino 



1 Ayubu adalumbira kuti adzamenya mkazi wake ndi zikoti zingapo. Ndipo 
Mulungu adamasula kulumbira kwake kuti atenge mtolo wa zikoti zomwe 
m'kati mwake mudali chiwerengero chomwe adalumbirira kuti adzammenya 
nacho, ndipo ammenye ndi mtolowo kuti akwaniritse kulumbira kwakeko. Mulungu 
adamchitira chifundo chimenechi chifukwa chakuti adapirira pa masautso ake. 






%3#W$$fa 






Surat 38. Sad 



Juzu 23 



980 



tr *>» 



r a Jfi 5jj-- 



49. Ichi ndichikumbutso (kwa 
iwe ndi anthu Ako). Ndipo ndithu, 
oopa Mulungu Ali ndi mabwerero 
abwino. 

50. (Awakonzera iwo) minda 
yamuyaya Yotsekulidwa makomo 
Ake kwa iwo. 

51. (Azidzakhala m'menemo) 
uku Atatsamira (mabedi amtengo 
wapatali, Ndipo adzakhala 
akusangalala) Akuitanitsa 
mmenemo zipatso ndi Zakumwa 
zambiri; 

52. Ndipo (ku Munda wa 
Mtenderewo) Adzakhala ndi akazi 
oyang'ana amuna Awo okha basi, 
ofanana misinkhu. 

53. Izi ndi zomwe 
mukulonjezedwa pa tsiku 
Lachiweruzo. 

54. Ndithu, izi ndizopatsa Zathu 
Zosatha; 

55. Awa ndimalipiro (a oopa 
Mulungu)! Koma opyola malire 
(Ndi kunyoza aneneri awo), ali ndi 
Mabwerero oipa. 

56. (Omwe ndi) Jahannama 
adzailowa (ndi Kupsereramo). 
Taonani kuipa Choyala 
chimenecho! 

57. Awa ndimadzi wotentha 
kwambiri, Ndi mafinya (a anthu a 
kumoto). Choncho awalaweko! 









®&$^&J&te 



Ol^tAp^o^yUtoA 






«W$a£g 






^y^sfessu 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



981 



tr^i 



f A Jfi Sjj~- 



58. Ndi zilango zina zambiri 
Zonga zimenezi. 

59. (Kudzanenedwa kwa opyola 
malire, Omwe ndiatsogoleri a 
opembedza Mafano): "Gulu ili 
lalikulu, Lilowa nanu kumoto; 
(Omwe adali okutsatirani. Ndipo 
Atsogoleri adzati): Siolandiridwa 
(Mwamtendere). Ndithu, iwo 
ngolowa Kumoto. 

60. (Otsatira adzanena): 
"Ndithu, Tembereroli likuyenera 
inu, (Limene mukutitemberera ife) 
Chifukwa inu ndiamene 
mudadzetsa Chilangochi 
potinyenga ife (ndi Kutiitanira 
kunjira yopotoka), Taonani kuipa 
(Jahena) malo Okhazikikamo!" 

61. (Otsatira) adzanena, "O, 
Ambuye wathu! Muonjezereni 
chilango kumoto Pamwamba pa 
chilango amene Watidzetsera 
chilangochi." 

62. Ndipo (anthu akumoto) 
adzanena "Kodi nchifukwa ninji 
sitikuwaona Anthu aja omwe 
timawawerengera Kuti ngoipa 
(padziko lapansi)? 

63. Kodi bwanji timawachitira 
chipongwe(Padziko lapansi koma 
taonani sadalowe Nafe kumoto). 
Kapena kuti Maso athu sakuwaona?" 

64. Ndithu, zimenezo, 
Zokangana anthu Akumoto nzoona. 









w*&y loj&£»5f $&j>\yS 



^m% 4 &$%c$% 



4Z$^^Mj*£>'&\ 



*&$$&&&$>& 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



982 



yr *>i 



TA Jfi 5jj-*» 



65. Nena (kwa iwo): "Ndithu 
ine ndine M"chenjezi (wochenjeza 
za chilango Cha Mulungu). Palibe 
wopembedzedwa Mwachoonadi, 
koma Mulungu Mmodzi Yekha 
Wopambana; 

66. Mbuye wathambo ndi 
nthaka, ndi Zapakati pake; 
Wamphamvu zoposa; 
Wokhululuka machimo kwambiri 
(Kwa yemwe walapa ndi 
Kumkhululupirira)". 

67. Nena (kwa iwo iwe 
Mtumiki {SAW}): "Ichi (chimene 
ndakuchenjezani Nachochi) 
ndinkhani yaikulu, 

68. Inu, za chimenechi, 
mukunyozera! 

69. Sindimadziwa chilichonse 
za Akuluakulu a pamwamba 
(Angelo) pamene amakangana (Za 
kulengedwa kwa Adamu) 

70. Palibe china chimene 
Chavumbulutsidwa kwa ine, koma 
(Kuti ndikuuzeni mawu awa oti): 
"Ine Ndine mchenjezi (wanu) 
woonekera." 

71. Akumbutse pamene Mbuye 
wako Adanena kwa angelo: "Ine 
ndilenga Munthu kuchokera ku 
dothi,( Yemwe ndi Adamu). 

72. Ndikammaliza ndi 
Kumuuzira mzimu wochokera 



&jMky35#Gffa$ 



2$&<.rt 



'y&^J&fe^ 



®M 



<tefS8tf 









Surat 38. Sad 



Juzu 23 



983 



vr *jA-i 



TA Jfi 5jj-*» 



Kwa Ine, igwani pansi 
Momulemekeza. " 

73. Choncho angelo onse 
Anagwa pansi momulemekeza." 

74. Kupatula Iblis; adadzikuza, 
ndipo adali Mmodzi mwa 
osakhulupirira. 

75. (Mulungu) adati: "E, iwe 
Iblisa! Nchiyani chakuletsa kugwa 
pansi ndi Kuchilemekeza chimene 
ndachilenga ndi Manja anga 
(popanda kutuma wina)? 
Wadzikweza kapena uli mmodzi 
wa Odziika pamwamba?" 

76. (Iblis) adanena: "Ine ndine 
wabwino Kuposa iye (Adamu); 
chiftikwa ine Mudandilenga 
kuchokera kumoto, Ndipo iye 
mudamulenga Kuchokera kudongo." 

77. (Mulungu) adanena (kwa 
Iblis): "Tuluka m'menemo 
(m'gulu la angelo Apamwamba); 
ndithu, iwe Ngopirikitsidwa (ku 
chifiindo cha Mulungu). 

78. "Ndipo ndithu, 
matemberero Anga Akhala pa iwe 
kufikira Tsiku lamalipiro. 

79. (Iblis) adati: "O, Mbuye 
wanga! Ndipatseni nthawi kufikira 
tsiku Louka ku imfa." 

80. (Mulungu) adati: "Ndithu, 
iwe ndiwe Mmodzi wa 
wopatsidwa nthawi. 









%&#£$$&&% ™ 



Wasa&ftafrSfc 



%^2&U&x&Js 



h&j&\&$&'$> 



Surat 38. Sad 



Juzu 23 



984 



tr^i 



r a jfi ojj-i 



81. Kufikira tsiku la nthawi 
Yodziwika (imene yaikidwa)." 

82. (Iblis) adati: "Choncho 
kupyolera Muulemerero Wanu 
ndikulumbira kuti Ndiwasokoneza 
onse. 

83. Kupatula akapolo Anu 
omwe ali Osankhidwa mwa iwo. 
(Pa iwo Ndilibe nyonga zilizonse)." 

84. (Mulungu) adati: 
"Ndikulumbira Mwachoonadi 
ndipo Ndikunena choona. 

85. Ndithudi, ndidzadzazitsa 
Jahena ndi Ochokera ku mtundu 
wako Ndi omwe adzakutsate mwa 
Iwo (ana a Adamu), onse." 

86. Nena (iwe Mtumiki{SAW}, 
kwa Anthuako:) 
"Sindikupemphani Malipiro 
pazimenezi Ndiponso ine 
simmodzi wa Odzikakamiza (pa 
zinthu zosandiyenera,) 

87. (Qur'an) sichina koma 
ndichikumbutso Ndi chiphunzitso 
kwa zolengedwa zonse. 

88. Ndipo posachedwa 
mudziwa, (inu Otsutsa, kuona 
kwa) nkhani zake." 






t&SF*'™ 



'\f 6»<i *'^i» '$•" "<t<\ 



©<r&s^ji 



ev&&&£& 



4><£*«ftfgSaj 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 



985 



tfftjA-i r<\jAJ\ij^ 




Surayi idavumbulutsidwa ku Makka. Koma kukunenedwa 
kuti ma aya atatu nga ku Madina. Ndipo ma ayawo ndi awa: 52, 
53 ndi 54. 

Surayi yayamba ndi kunenetsa za ulemerero wa Qur'an. 
Ndipo kenako yaitanira ku zopembedza Mulungu Mmodzi ndi 
kuwatsutsa omwe akunena kuti Chauta ali ndi mwana. 

Kenako yakamba za kukhoza kwa Mulungu mkalengedwe ka 
kumwamba ndi pansi, ndi mkalengedwe ka anthu. Ndi 
kunenetsa kuti anthu ngati amkana, lye Ngodzikwaniritsa ndipo 
palibe chimene akusaukira kwa iwo. Ndipo ngati amthokoza, 
akuyanja kuthokoza kwawo. Koma sayanja kum'kana. 

Yakambanso za chikhalidwe cha munthu mmalo awiri, 
ponena kuti iye mavuto akamkhudza, amampempha Mbuye 
wake ndi kutembenukira kwa Iye modzichepetsa. Koma 
akampatsa mtendere amaiwala zomwe adali kupempha kale ndi 
zomwe zidampeza. 

Ndipo yawakumbutsa chisomo cha Mulungu chomwe chili pa 
iwo powatsitsira madzi kuchokera kumwamba omwe akutulutsa 
chakudya chawo ndi chakudya cha ziweto zawo. Pazimenezi 
pali phunziro ndi chikumbutso kwa eni nzeru. 

Kenako surayi ikubwerezanso pofotokoza za Qur'an za 
kulowerera m'mitima ya omwe akuopa Chauta, ndikuti Mulungu 
wapereka mafanizo osiyanasiyana mmenemo kuti anthu 
alingalire za Mulungu. Ndipo kenako yafanizanso pakati pa 
munthu wopembedza mafano ndi yemwe akupembedza Mulungu 
Mmodzi, ndikunena kuti iwo sali ofanana. Ndipo yanenanso kuti 
imfa ndi wo malekezero a onse. 

Yafotokozanso za mabwerero a omwe akutsutsa Mulungu ndi 
kutsutsa choona. Ndi mabwerero a olungama mzolankhula zawo, 
amene akuvomereza zomwe Chauta wavumbulutsa kwa iwo. Ndipo 
yatinso kuti mukawafunsa awa opembedza mafano kuti: "Ndani 
adalenga thambo ndi nthaka?" Ayankha kuti: "Ndi Mulungu." 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 986 tr *>» r* yjJi 5j>- 



Koma iwo kuonjezera pa zimenezo, akupembedza zina 
kusiya Mulungu; zimene sizingawateteze ku chilango cha 
Mulungu ngati Mulungu atafuna kuwalanga. Ndipo sizingaletse 
chifundo cha Chauta pa iwo ngati lye atawachitira chifundo. 

Surayi ikunenetsa kuti Bukuli lavumbulutsidwa mwa choona. 
Ndipo yemwe aongoke nalo, ubwino wake uli pa iye mwini. 
Ndipo amene akhote, uchimo wake uli pa iye mwini. Ndipo 
udindo wa Mtumiki ndi kufikitsa uthenga basi, osati kukakamiza 
anthu. 

Surayi yabwerezanso kukumbutsa zouka ku imfa ndi za 
Amushirikina amene adadzipangira milungu yabodza imene 
siingawateteze chilichonse. 

Pamene yafotokoza mwatsatanetsatane za zoipa za onyoza 
opyola malire, zomwe akonzedwera pa tsiku lomaliza, monga 
chilango chowawa, yafotokozanso za chifundo chochuluka cha 
Mulungu kuti asataye mtima, ponena kuti, "E, inu anthu Anga, 
amene mwapyola malire podzichitira nokha zoipa! Musataye 
mtima ndi chifundo cha Mulungu. Ndithu, Mulungu 
amakhululuka machimo onse; Iye Ngokhululuka kwabasi, 
Wachifundo Chambiri." Ndipo yawaitana kuti atembenukire 
kwa Iye, chilango chisanawadzere mowadzidzimutsa. 

Ndipo tsiku la Kiyama udzaona nkhope zawo, amene 
adatsutsa Mulungu, zili zodandaula. Koma amene adaopa 
Chauta, zoipa sizidzawakhudza. 

Surayi yatsiriza ndi kukamba za tsiku la chitsiriziro. 
Kuyamba kwake, nkuimbidwa lipenga lomwe lidzakomola onse 
a kumwamba ndi pansi, kupatula amene Mulungu wafuna, 
kufikira pom we aliyense adzalandira chomwe ayenerana nacho. 
Anthu a kumoto, kunka ku moto; a ku munda wa mtendere, 
kunka ku mtendere. Ndipo anthu a ku munda wa mtendere 
adzanena ali m'Mundamo: "Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu, Yemwe watitsimikizira lonjezo Lake; waweruza pakati 
pa onse mwa choona." Ndipo kudzanenedwanso, "Kuyamikidwa 
konse nkwa Mulungu, Mbuye wa zolengedwa." 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 987 tr *>i 



r\ >ijji ij^ 



5«ra/ Az-Zumar XXXIX 



mm < 



7v ■: 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuvumbulutsidwa kwa Buku 
ili Kwachokera kwa Mulungu, 
Mwini Mphamvu zoposa; Mwini 
Nzeru zakuya. 

2. Ndithu, Ife takuvumbulutsira 
iwe Buku ili mwamtheradi; choncho 
Mpembedze Mulungu Momyeretsera 
mapemphero lye yekha. 

3. Dziwani kuti Mulungu 
Ngolandira Mapemphero oyera, 
(opanda Kuphatikizidwa ndi zina). 
Koma Amene adzipangira 
athandizi Kusiya Mulungu, 
(akumanena kuti):"Ife 
sitikuwapembedza awa, koma 
Tikutero ndi cholinga choti 
Atifikitse pafupi ndi Mulungu." 
Ndithu, Mulungu, adzaweruza 
Pakati pawo (pakati pa 
okhulupirira Mulungu, ndi okana) 
pa zimene Akusiyana. Ndithu, 
Mulungu saongola Amene ali 
wabodza; wokanira (Mulungu). 

4. Mulungu akadafuna kupeza 
mwana, Akadasankha yemwe 
akum'funa Mzomwe adalenga. 
Wapatukana Ndi zimenezo! lye ndi 
Mulungu Mmodzi; Wopambana; 
Wochita zimene Wafuna. 



oi^l^J^U- 



-^ 



®j&m^^&# 









a* 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 I 988 I tV ^ 



x% j^jit o^j— 



5. Adalenga thambo ndi nthaka 
Mwamtheradi.Amakulunga usiku 
Mu usana; ndipo amakulunga 
usana Mu usiku. Ndipo dzuwa ndi 
mwezi Wazichita kuti zitumikire 
monga momwe Afunira. Zonsezi 
zikuyenda kufikira Pa nthawi yake 
imene yaikidwa. Dziwani kuti lye 
(Mulungu) Ngwamphamvu 
zoposa; Ngokhululuka Kwambiri. 

6. Adakulengani kuchokera mu 
mzimu Umodzi (womwe ndi 
Adamu; tate wa Anthu). Ndipo 
kenako adalenga Kuchokera mu 
mzimu umenewo Mnzake, (mkazi 
wake, Hawa); 

ndipo Adakutsitsirani mitundu 
isanu ndi itatu Ya nyama 
ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira 
yaimuna ndi yaikazi, ng'ombe 
Yaimuna ndi yaikazi, mbuzi 
yaimuna Ndi yaikazi ndi nkhosa 
yaimuna ndi Yaikazi. Zonse 
pamodzi, zisanu ndi Zitatu, zomwe 
mumathandizidwa Nazo kwambiri). 
Amakuumbani Mmimba mwa mayi 
anu mkaumbidwe Kosiyanasiyana, 
mu mdima utatu; (Mu mdima wa 
mimba, chiberekero Ndi mdima 
wa membuleni). Ameneyo 
(Adakuchitirani zonsezi), ndi 
Mulungu, Mleri wanu; ufiimu Ngwa 
lye. Palibe Wopembedzedwa mwa 
choona, koma lye. Kodi nanga 
mukutembunuzidwa Bwanji kusiya 
Mulungu? 









Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 



989 



rr t^r\ 



T^ yjil 5jj-j 



7. Ngati mukana ndithu, 
Mulungu Ngodzikwaniritsa 
sasaukira kwa inu (Chikhulupiriro 
chanu ndi kuthokoza Kwanu); 
koma sakonda kukanira kwa Anthu 
Ake.Ngati mumthokoza (Pa 
mtendere Wake umene uli pa inu) 
Akuyanja kuthokoza kwanuko. 
Ndipo Mzimu wochimwa 
sungasenze machimo A mzimu 
wina. Kenako kobwerera Kwanu 
nkwa Mbuye wanu, ndipo 
Adzakuuzani zimene mudali 
kuchita. Ndithu, lye Ngodziwa 
zinsinsi Za mmitima. 

8. Ndipo masautso akampeza 
munthu, Amapempha Mbuye wake 
ndi Kutembenukira kwa lye 
(pomwe Chikhalirecho adali 
kumnyoza). Kenako (Mbuye 
wake) akampatsa mtendere 
Wochokera kwa lye (waukulu), 
Amaiwala (masautso aja) omwe 
adali Kumpempha Mulungu kuti 
amchotsereAsadampatse 
mtenderewo, ndipo Kenako 
ndikumpangira Mulungu Milungu 
inzake kuti adzisokeretse iye 
Mwini (pamodzi ndi ena) 
Kuchokera ku njira ya Mulungu. 
Nena(Iwe Mtumiki kwa Yemwe 
ali ndi Chikhalidwe chotere): 
Sangalala ndi Kukanira kwako 
(mtendere wa Mulungu) kwa 
nthawi yochepa. Ndithu, Iwe ndi 
mmodzi wa anthu aku moto. 









Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 



990 



tr ftjJt-i 



r<* yjii s^ 



9. Kodi yemwe akudzichepetsa 
(kwa Mulungu ndi kumpembedza) 
pakati pa Usiku uku akugwetsa 
nkhope pansi Ndi kuimirira, 
kuopa tsiku la Chimaliziro ndi 
kuyembekezera Chifundo cha 
Mbuye wake,(kodi Angafanane ndi 
yemwe amapempha Mulungu 
akakhala pa mavuto pokha, 
Akakhala pa mtendere 
ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, 
iwe Mtumiki {SAW}): "Kodi 
amene akudziwa ndi amene 
Sakudziwa, ngofanana?" Ndithu, 
ndi eni Nzeru amene amalingalira. 

10. Nena (kwa iwo mau Anga 
akuti): "E, inu Akapolo Anga 
amene mwakhulupirira! Muopeni 
Mbuye wanu. Ndithu,Amene 
achita zabwino zotsatira zake 
Nzabwino padziko lapansi ndipo 
Dziko la Mulungu ndilophanuka. 
(Pirirani chifukwa chosiya midzi 
yanu Ndi abale). Ndithu, opirira 
adzalipidwa Malipiro awo 
mokwana Mopanda mulingo." 

11. Nena: "Ine ndalamulidwa 
kuti Ndipembedze Mulungu 
momuyeretsera Mapemphero Ake 
(posam'phatikiza Ndi aliyense pa 
mapemphero, kapena Kupemphera 
mwa chiphamaso)." 

12. "Ndalamulidwanso kuti 
ndikhale Woyamba mwaogonjera 
(Malamulo Ake)" 









^&&\$&M$ 



u'-TK 



®ti^\'$£$&M3 



Siirat 39. Az-Zumar Juzu 23 



991 



tr *>» 



rs yjiidjj-- 



13. Nena: "Ine ndikuopa 
Chilango cha tsiku lalikulu, 
(Loopsa), ngati ndinyoza Mbuye 
wanga." 

14. Nena (kwa iwo, iwe 
Mneneri{SAW}): "Ndi Mulungu 
Yekha ndikumpembedza 
Pomuyeretsera lye mapemphero 
anga. 

15. Choncho pembedzani 
zimene mwafuna, Kumsiya lye." 
Nena (kwa iwo): "Ndithu, Otaika 
ndi kuonongeka kwakukulu,Ndi 
amene adzitaya okha, (adziluzitsa 
Okha), ndi maanja awo, patsiku la 
Kiyama. Dziwa, ndithu, kumeneko 
Ndiko kuluza koonekera. 

16. Pa iwo padzakhala 
misanjikosanjikoYa moto 
ndiponso pansi pawo. Ndi chilango 
chimenechi, Mulungu 
Akuwaopseza nacho akapolo Ake. 
"E, inu akapolo AngalNdiopeni! 

17. Ndipo amene apatukana 
nawo mafano ndi Satana posiya 
kuzipembedza, ndikusiya 
Kuziyandikira, ndipo mmalo 
mwake Nkutembenukira kwa 
Mulungu (Pazochita zawo zonse), 
nkhaniYabwino njawo 
(ponseponse). Auze nkhani 
yabwino akapolo Anga. 

18. Amene akumvetsera mawu 
Ndikutsatira amene ali abwino 



'\f 9»s 9 9 " >i;.r >"r^r i ?\2 















&$. 



*>''%^'&6s&&\ 



Siirat 39. Az-Zumar Juzu 23 



992 



rr *>i 



r^ yjit djj~» 



Kwambiri (ndi oongolera ku 
Choona.) I wo wo ndi Amene 
Mulungu wawaongola.Ndipo 
iwowo ndiwo eni nzeru. 

19. Kodi yemwe chiweruzo cha 
chilango Chatsimikizika pa iye, 
(mungamteteze)? Kodi iwe 
ungampulumutse yemwe Ali 
mmoto? 

20. Koma amene aopa Mbuye 
Wawo, iwo adzakhala nazo 
Nyumba zikuluzikulu zimene 
Zamangidwa mosanjikizana, 
Mitsinje ikuyenda pansi Pake. Hi 
ndi lonjezo lochokera kwa 
Mulungix Mulungu saphwanya 
lonjezo. 

21. Kodi suona kuti Mulungu 
amatsitsa Madzi kuchokera 
kumwamba, ndipo Amawalowetsa 
mu akasupe mkati Mwanthaka. 
Kenako amatulutsa ndi Madziwo 
mbewu zosiyana Mitundu: 
(chimanga, mpunga, Tirigu, ndi 
zina zotere). Ndipo kenako 
Imauma (pambuyo pokhala 
yobiriwira); Umaiona ili ya 
chikasu. Kenako Amaichita 
kukhala zidutswazidutswa. 
Ndithu, muzimenezo Muli 
chikumbutso kwa Eni nzeru 
(zofufuzira zinthu). 

22. Kodi amene Mulungu 
watsekula Chifuwa chake 















&&jtta&&l&&v& 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 



993 



rr *>» 



V^ ^»jJl ^jj-*' 



povomereza Chisilamu, Kotero 
kuti iye akuyenda mkuunika Kwa 
Mbuye wake, (angafanane ndi 
Yemwe akunyozera kupenyetsetsa 
Zisonyezo za Mulungu?) 
Kuonongeka Kwakukulu kuli pa 
ouma mitima yawo 
Posakumbukira Mulungu (ndi 
kulabadira Qur'an). Iwo ali 
m'kusokera koonekera. 

23. Mulungu wavumbulutsa 
nkhani yabwino Yomwe ndi Buku 
logwirizana nkhani Zake; 
(losasemphana). 
Lobwerezabwereza (malamulo 
ake). Makungu a omwe amaopa 
Mbuye Wawo amanjenjemera ndi 
ilo. Kenako Makungu awo ndi 
mitima yawo Zimakhazikika 
pokumbukira Mulungu. Buku 
limeneli ndi chiongoko cha 
Mulungu; ndi ilo, akumuongola 
ameneWamfuna. Ndipo amene 
Mulungu Wamulekerera kuti 
asokere (chifukwa Chonyozera 
kwake choona), sangakhaleNdi 
womuongola (ndi ompulumutsa 
Ku chionongeko). 

24. Kodi yemwe adzakhala 
akudzitchinjiriza Ndi nkhope yake 
(uku manja atanjatidwa) Ku 
chilango choipa pa tsiku la 
Kiyama, (Angafanane ndi yemwe 
adzakhala Mchisangalalo mminda 
ya mtendere?" Ndipo 









»~&<. *"<t 






'W 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 23 



994 



rr *>i 



V^ yj\ $jj-» 



kudzanenedwa kwa oipa:"Lawani 
zoipa za zochita zanu." 

25. Amene adalipo patsogolo 
pawo, Adatsutsa.Ndipo Chilango 
chidawadzera Kuchokera momwe 
sadali Kuyembekezeramo. 

26. Choncho Mulungu 
adawalawitsa Kunyozeka pamoyo 
wa padziko Lapansi; koma, ndithu, 
chilango cha Tsiku la chimaliziro 
nchachikulu zedi (Kuposa chilango 
cham'dziko Lapansi) akadakhala 
akudziwa! 

27. Ndithu, m'buku ili la 
Qur'an Taperekamo mafanizo 
osiyanasiyana Kwa anthu kuti 
akumbukire. 

28. Qur'an ya Chiarabu 
Yopanda zokhota, kuti Iwo aope 
(Mulungu). 

29. Mulungu wakupatsani 
Fanizo la munthu Wotumikira 
mabwana awiri omwe Ngokangana 
pa za iye, ndi munthu Yemwe 
akutumikira bwana mmodzi. Kodi 
awiriwa ngofanana? Kuyamikidwa 
konse nkwa Mulungu! Koma 
ambiri a iwo sadziwa. 

30. Ndithu, iwe udzafa; Naonso 
adzafa. 

31. (Ndipo) kenako, inu patsiku 
La Kiyama m'dzakangana Kwa 
Mbuye wanu. 



AC^Sp^i^S &(£$\ oOo 


















Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



995 I * i *>■ 



f^ ^jJl 5jj-*> 



32. Kodi ndiyani wachinyengo 
Wamkulu woposa yemwe 
Akumnamizira Mulungu Zabodza, 
ndi kutsutsa choona Chikamdzera? 
Kodi Jahannama Simalo a okanira? 

33. Ndipo amene wadza ndi 
choona, Naachikhulupirira, iwowo 
ndiwo Oopa Mulungu. 

34. Adzapeza zomwe 
adzakhumba kwa Mbuye wawo. 
Imeneyo ndiyo mphoto Ya ochita 
zabwino. 

35. Kuti Mulungu awafafanizire 
Zoipa za zochita zawo, Ndi kuti 
awalipire malipiro Awo chifukwa 
cha zabwino Zomwe adali kuchita. 

36. Kodi Mulungu sali 
Wokwanira kwa kapolo Wake? 
Koma akukuopseza ndi Zina 
zomwe similungu! Ndipo yemwe 
Mulungu wam'lekerera kuti 
asokere, Ndithu, alibe 
womuongola. 

37. Ndipo amene Mulungu 
Wamuongola, palibe amene 
Angathe kumsokeretsa. Kodi 
Mulungu sali Mwini Mphamvu 
Zoposa; Wokhoza kubwezera 
chilango? 

38. Ndipo ukawafunsa (kuti) 
ndani Adalenga thambo ndi • 
nthaka, ndithu, Anena (kuti ndi) 
"Mulungu". Nena: "Kodi mukuona 





















Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



996 



rt cjA-i 



r* yjji Sj^ 



bwanji, amene Mukuwapembedza 
kusiya Mulungu Angandichotsere 
masautso ake ngati Mulungu 
atafuna kundipatsa masautso? 
Kapena Mulungu atafuna 
kundichitira Chifundo, kodi iwo 
angatsekereze Chifundo 
Chakecho?" Nena: "Mulungu 
akundikwanira! Kwa lye, atsamire 
otsamira." 

39. Nena: "E, inu anthu anga! 
Chitani Zochita zanu mmene 
mungathere. Nanenso ndichita 
(mmene Ndingathere). Koma 
posachedwa mudziwa. 

40. Amene chim'dzere chilango 
Chomuyalutsa,ndi kum'fikira iye 
Chilango chamuyaya." 

41. Ndithu, Ife 
takuvumbulutsira Buku ili 
Chifukwa cha anthu (onse) kuti 
Tiwafotokozere choona. Choncho 
Amene waongoka, zabwino zake 
nza iye Mwini.Koma amene 
wakhota, ndiye Kuti 
akudzikhotetsa yekha. (Ndipo 
Zoipa za kukhotako zidzakhala pa 
iye Yekha). Ndipo iwe sikapitawo 
wawo. 

42. Mulungu ndiye amatenga 
mizimu pa Nthawi ya imfa yake 
ndipo amatenga Mizimu yomwe 
siidafe panthawi Yogona 
tulo.Ndipo amaigwira mizimu 












Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



997 



t£ ij*r\ 



T^ j*£\ *JJ** 



Imene wailamula kufa, 
(osaibwezera Ku matupi awo). 
Koma inayo Amaitumiza 
(kumatupi awo, yomwe Nthawi 
yake siidakwane) kuti Ikwaniritse 
nthawi yake imene Idaikidwa. 
Ndithu, m'zimenezi muli 
Zisonyezo kwa anthu olingalira. 

43. Kodi adzipangira 
Apulumutsi kusiya Mulungu? 
Nena: "Ngakhale kuti 
(Apulumutsiwo) alibe mphamvu 
ndi Kuzindikira pa chilichonse?" 

44. Nena: "Chiombolo chonse 
chili kwa Mulungu; Ufumu wa 
kumwamba ndi Pansi Ngwake; 
kenako kwa lye M'dzabwezedwa." 

45. Ndipo pamene Mulungu 
Yekha Akutchulidwa,mitima ya 
amene Sakhulupirira tsiku la 
chimaliziro Imanyansidwa; koma 
akatchulidwa Amene sali lye, iwo 
amakondwa. 

46. Nena: "E, Ambuye! Mlengi 
wa thambo ndi Nthaka! Wodziwa 
zobisika ndi Zoonekallnu 
mudzaweruza pakati pa Akapolo 
Anu pa zimene adali 
Kusemphana." 

47. Ndipo amene adzichitira 
zoipa, ngakhale Kukadakhala kuti 
ali nazo zonse Zamnthaka pamodzi 
ndi zina zonga izo, Kuti 






e&F* 






©<z£ 






Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 998 1 t *>i 



**j>Phy* 



adziombole nazo ku chilango 
choipa Cha tsiku la Kiyama, 
(sizingavomerezedwe). Ndipo 
zidzawaonekera kuchokera kwa 
Mulungu, zomwe sadali 
kuziyembekezera. 

48. Kukawaonekera kuipa Kwa 
zimene adazichita, Ndipo 
zikawazinga zimene Adali 
kuzichitira chipongwe. 

49. Pamene munthu mavuto 
amkhudza, Amatipempha (uku ali 
wodzichepetsa); Koma tikampatsa 
mtendere wochokera Kwa Ife, 
amanena kuti: "Ndapatsidwa 
Mtendere uwu chifukwa 
chakudziwa Kwanga (njira 
zoupezera)." (Sichoncho) Koma 
mtendere umenewu ndi mayeso; 
Koma ambiri a iwo sadziwa! 

50. Ndithu adanenanso zonga 
Zimenezi omwe adalipo Patsogolo 
pawo, koma Sizidawathandize 
zimene Adali kuchita. 

51. Choncho, zidawapeza Zoipa 
za zomwe adazichita. Ndipo 
amene achita chinyengo Mwa awa, 
posachedwa kuwapeza Kuipa kwa 
zomwe achita, Ndipo iwo 
sangamlempheretse (Mulungu). 

52. Kodi iwo sadziwa kuti 
Mulungu Akuchulukitsira zopatsa 
Zake yemwe Wamfuna, ndi 



©£^s$#u*u* 



9 . i**' '\99"{\' 9\*' 99\\"" 



***<*' 






Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



999 



rt »>i 



r* ^jJt Sj^- 



kumchepetsera (amene Wamfuna)? 
Ndithu, m'zimenezi muli 
Malingaliro kwa anthu okhulupirira. 

53. Nena (kwa iwo mau anga 
akuti): "E, inu Akapolo anga! 
Amene Mwadzichitira chinyengo, 
musataye Mtima ndi chifundo cha 
Mulungu. Ndithu, Mulungu 
amakhululuka Machimo onse. 
Ndithu, lye Ngokhululuka 
kwambiri, Wachisoni. 

54. Ndipo tembenukirani Kwa 
Mbuye wanu, Ndipo m'gonjereni 
chilango Chisadakudzereni. Ndipo 
zitatero, Sim'dzapulumutsidwa. 

55. Ndipo tsatirani zabwino, 
zimene Zavumbulutsidwa kwa inu 
kuchokera Kwa Mbuye wanu 
chisadakufikeni Chilango 
mwadzidzidzi pomwe inu 
Simkudziwa!" 

56. Kuti mzimu usazanene: 
"Kalanga ine! Mzomwe 
sindidalabadire kumbali ya 
Mulungu; ndithu, ndidali mmodzi 
wa Ochitira chibwana (zinthu za 
Chipembedzo)." 

57. Kapena ungazanene: 
"Mulungu Akadandiongola, 
ndithu, ndikadakhala Mwa oopa 
Mulungu." 

58. Kapena kunena utaona 
chilango: "Ndikadatha kubwerera 



&, 



*z *>* 















Siirat 39. Az-Zumar Juzu 24 iQOO * * *>' 



f^ jA^\ OjJ-rf 



(Padziko lapansi), ndikadakhala 
Mmodzi wa ochita zabwino." 

59. (Adzauzidwa: "Nchiyani 
iwe?) Ndithu, zidakufika 
zisonyezo Zanga, ndipo 
udazitsutsa ndi Kudzitukumula; 
ndipo Udali mmodzi wa okanira." 

60. Ndipo tsiku la Kiyama 
Udzawaona omwe adamnamizira 
Mulungu, nkhope zawo zili 
zakuda. Kodi Jahannama simalo a 
Odzitukumula? 

61. Ndipo Mulungu 
adzawapulumutsa Amene 
adamuopa, chifukwa cha 
Kupambana kwawo. Zoipa 
Sizikawakhudza, ndipo iwo 
Sakadandaula. 

62. Mulungu ndiye Mlengi wa 
chilichonse, Ndipo lye ndi 
Myang'aniri wa Chilichonse. 

63. Makiyi a kumwamba ndi 
Pansi ali kwa lye. Ndipo Amene 
akanira zisonyezo za Mulungu, 
iwo ndi wo oluza, (otaika). 

64. Nena: "Kodi 
mukundilamula Kuti ndipembedze 
yemwe Sali Mulungu, E, inu mbuli?" 

65. Ndipo ndithu, 
kwavumbulutsidwa Kwa iwe, ndi 
kwa amene adalipo Patsogolo pako 
(mawu awa:) "Ngati umphatikiza 
(Mulungu ndi milungu yabodza), 















Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



1001 



Yt *>» 



r<i yjji o^ 



Ndithu ntchito zako Zionongeka, 
ndipo Ukhala mwa oluza (otaika)." 

66. Koma pembedza Mulungu 
yekha, ndipo Khala mwa othokoza. 

67. Koma sadamlemekeze 
Mulungu, Kulemekeza koyenerana 
Naye, pomwe Patsiku la Kiyama 
nthaka yonse (Idzakhala), 
chofumbata Chake mmanja; ndipo 
thambo Lidzakulungidwa ndi 
Dzanja lake lamanja. 
Walemekezeka Mulungu. Ndipo 
watukuka Kuzimene 
akum'phatikiza nazozi. 

68. Ndipo (pamene) lipenga 
lidzaimbidwa, Onse a kumwamba 
ndi pansi Adzakomoka kupatula 
amene Mulungu Wamfuna.Kenako 
lidzaimbidwa Lachiwiri; 
pamenepo (onse) adzauka; 
Adzakhala akuyang'ana 
(modabwa: 'Nchiyani chachitika!). 

69. Ndipo nthaka (tsiku 
limenelo) idzawala Ndi kuunika 
kwa Mbuye wake; Ndipo 
akaundula a zochita, adzaikidwa. 
Ndipo adzabweretsedwa aneneri 
ndi Mboni (kuti aikire umboni pa 
anthu). Ndipo padzaweruzidwa 
pakati pawo Mwachoonadi; ndipo 
iwo Sadzaponderezedwa. 

70. Ndipo mzimu uliwonse 
Udzalipidwa zimene udachita; 












y^% oi^i^^^ ^$L 



Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 1002 * * *j*-' 



T^ yj\ 5jj-» 



Ndipo lye (Mulungu) Ngodziwa 
kwambiri zimene akuchita. 

71. Ndipo amene adakanira, 
adzakusidwa Ku Jahena ali 
magulumagulu kufikira Pomwe 
adzaifikira, makomo ake 
Adzatsekulidwa, ndipo alonda ake 
Adzawauza: "Kodi sadakudzereni 
aneneri Ochokera mwa inu 
okulakatulirani Zisonyezo za 
Mbuye warm, ndi Kukuchenjezani 
za kukumana kwanu Ndi tsiku 
lanuli?" Adzayankha (nati): "Inde, 
adatidzera; koma lidatsimikizika 
Liwu la chilango pa okanira." 

72. Kudzanenedwa: "Lowani 
makomo a ku Jahannama; 
mukakhale mmenemo 
Muyaya.Taonani kuipa malo a 
odzitukumula! 

73. Ndipo amene adamuopa 
Mbuye wawo, Adzakusidwa kunka 
ku Munda wa Mtendere ali 
magulumagulu, mpaka Kufikira 
pomwe adzaufika. (Adzapeza 
Kuti) makomo ake atsekulidwa. 
Alonda ake adzanena kwa iwo: 
"Mtendere ukhale pa inu 
kondwani! Lowani mmenemo, 
khalani muyaya." 

74. Ndipo iwo adzanena: 
"Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu, Amene Watitsimikizira 
lonjezo Lake, ndipo Watipatsa 



© 















Surat 39. Az-Zumar Juzu 24 



1003 * £ *>i 



r* ^jHojj- 



dziko (potipatsa kuti N'lathulathu). 
Tikukhala m'minda ya Mtendereyi 
paliponse tafuna. Taonani Kukoma 
malipiro aochitazabwino!" 

75. Ndipo udzaona angelo 
atazungulira Mphepete mwa 
Mpando Wachifumu Uku 
akulemekeza ndi kutamanda 
Mbuye wawo. Ndipo 
padzaweruzidwa Pakati pawo 
mwachoonadi, ndipo 
Kudzanenedwa (ndi zolengedwa 
zonse): "Kuyamikidwa nkwa 
Mulungu, Mbuye wa 
zolengedwa!" 



©^ij&2#$&££*!3i 







Surat 40. Ghafir Juzu 24 



1004 



Y i »j*-l i . jSlP «j>- 




SURAT GHAFIR XL ^^^^B 1 



Surayi yayamba ndi zilembo ziwiri za alifabeti, ndipo 
yayamba ndi kufotokoza za ulemerero wa Qur'an ponenetsa kuti 
idavumbulutsidwa kuchokera kwa Mwini Mphamvu zoposa; 
Mwini kudziwa kwambiri; Wokhululuka machimo; Wolandira 
kulapa kwa akapolo Ake; Wopereka chilango choopsa kwa 
onyoza; Mwini kupereka Mtendere. 

Kenako yaitanira ku Umodzi wa Mulungu, ndikuti pasakhale 
kunyengedwa ndi ulemerero ndi chuma cha anthu okanira 
Chauta. Ndipo yawaitana kuti akumbukire mapeto a anthu akale 
ndi zomwe zidawapeza pamene adanyoza aneneri awo. 

Yafotokozanso za angero amene akusenza mpando Wachifumu 
wa Mulungu ndi kumlemekeza kwawo ndi mapemphero awo. 
Ndipo yafotokozanso za mkwiyo wa Mulungu 
umene umakhala pa okanira. 

Mmalo mwambiri, Surayi yafotokoza zododometsa za Mulungu 
ndi kukhoza Kwake koposa komwe kuli mwa iwo eni ndiponso 
kumwamba ndi pansi. Ndiponso yafotokoza za mtendere umene 
apatsidwa. Ndipo yawalangizanso mma ayah ochuluka kuti 
amuyeretsere Chauta chipembedzo Chake. Ndipo mma ayah 
ambiri a Surayi muli mawu okumbutsa za tsiku lomaliza. 

Yafotokozanso za nkhani ya Musa pamodzi ndi Farawo ndi 
anthu ake, makamaka za okhulupirira a kubanja la Farawo. 
Ndipo kenako, yalangiza anthu kuti aziyendayenda padziko ndi 
kuyang'ana zilango zimene zidawatsikira anthu akale, ndikuti 
mapeto a kunyengedwa ndi zamdziko adali otani! 

Pamene chilango cha Mulungu chidawatsikira, adati: 
"Takhulupirira Mulungu Mmodzi yekha; tikuikana milungu 
tidali kuipembedza ija. Koma iwo adakhulupirira nthawi 
yoyenera kukhulupirira itatha. Choncho chikhulupiriro chawo 
sichidawathandize chilichonse. 

Imeneyi ndiyo njira ya Mulungu pa zolengedwa Zake. Panjira 
za Mulungu sungapezepo kusintha kulikonse chilango chikatsika. 
Choncho panthawiyo adaonongeka okanira Mulungu. 



Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1005 ***>» 



t ♦ J\* Ojj-u 



Surat Ghafir XL 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ha-Mim. 

2. Kuvumbulutsidwa kwa Buku 
(ili) Kwachokera kwa Mulungu 
Wamphamvu Zoposa; Wodziwa 
kwambiri. 

3. Wokhululukira machimo; 
Wolandira Kulapa (kwa yemwe 
walapa); Wolanga Mwaukali (kwa 
yemwe Wapitiriza kunyoza 
Mulungu); Mwini Kupereka 
mtendere. Palibe Wopembedzedwa 
mwa choona, Koma lye; 
kobwerera nkwa lye. 

4. Sangatsutsane pa zisonyezo 
za Mulungu Kupatula amene 
akanira. Choncho Kusakunyenge 
kuyendayenda kwawo Padziko 
(kunka nachita malonda ndi 
Kupeza phindu lalikulu ndi 
malondawo Popanda chovuta; 
posachedwa Tiwalanga). 

5. Iwo kulibe, anthu a Nuhi 
adakaniranso Pamodzi ndi 
makamu a anthu omwe Adali kuda 
aneneri, m'badwo wa Nuh Utatha; 
Ndipo m'badwo uliwonse Udaikira 
mtima kuchita choipa pa Mneneri 
wawo kuti am 'g wire (ndi 






Qfa&\vP$\&\j 



-a 



6^ 



W^*&V»3f* 















Surat 40. Ghafir Juzu 24 



1006 



rt *>» 



t • jdlP *jy** 



Kumupha). Adali kutsutsana 
Poteteza chachabe kuti ndi uwo 
(mtsutso Wawowo) achotse 
choona. Ndipo Ndidawaononga 
kotheratu. Tayang'ana, Chidali 
bwanji chilango changa (pa iwo!) 

6. Chonchonso latsimikizika 
liwu la chilango Pa okukanira (iwe 
Mtumiki{SAW}) Chifukwa iwo 
ndi anthu A kumoto (chifukwa 
chosankha Kukanira ndi kusiya 
kukhulupirira). 

7. Amene akusenza Mpando 
Wachifumu Ndi amene ali 
mmphepete mwake, Akulemekeza 
ndi kutamanda Mbuye Wawo, 
ndiponso akumkhulupirira lye; 
ndipo akupemphera chikhululuko 
Amene akhulupirira (ponena kuti): 
"E, Mbuye wathu! Chifundo ndi 
Kudziwa kwanu kwakwanira pa 
Chinthu chilichonse. Khululukirani 
Amene alapa ndi kutsatira njira 
Yanu; Ndipo apewetseni ku 
chilango cha Jahena! 

8. E, Mbuye wathu! Alowetseni 
ku Minda ya muyaya imene 
Mudawalonjeza.Ndi amene 
Adachita zabwino mwa atate Awo 
ndi akazi awo ndi ana awo. Ndithu, 
inu ndi Amphamvu Zoposa; 
Anzeru zakuya. 

9. Ndipo apewetseni ku zoipa; 
tsono Amene mudzampewetsa Ku 



%&#&» 









> t* * "X ' >" ri^"' 



^&&w&t# 



Surat 40. Ghafir Juzu 24 1007 * i *>i 



i * j31p Sjj-*' 



zoipa tsiku limenelo, Ndiye kuti 
mwamchitira Chifundo.Ndipo 
kumeneko Ndiko kupambana 
kwakukulu." 

10. Ndithu, amene akanira 
adzaitanidwa (Ndi kuuzidwa kuti): 
"Mkwiyo wa Mulungu pa inu udali 
waukulu kuposa Mkwiyo wanu pa 
mitima yanu (yomwe 
Yakulowetsani ku chilango) 
pamene Mudali kuitanidwa ku 
chikhulupiriro, (Ku Chisilamu); 
ndipo mudali kukanira. 

11. Adzanena: "E, Mbuye 
wathu! Mudatipatsa imfa kawiri: 
(Imfa Yoyamba, tisanabadwe. 
Ndipo imfa ya Chiwiri, padziko). 
Ndipo mudatipatsa Moyo kawiri: 
(Moyo woyamba wa Padziko 
lapansi. Ndipo moyo Wachiwiri 
wakuuka kwa akufa). Choncho 
tavomereza machimo athu. Kodi 
pali njira yotulukira (Ku chilango 
kuno)? 

12. Zimenezi nchifukwa chakuti 
Akapembedzedwa Mulungu 
Mmodzi, mudali kutsutsa. Koma 
akaphatikizidwa (Ndi milungu 
yabodza) mudali 

Kukhulupirira.Choncho chiweruzo 
ncha Mulungu, Wotukuka, 
Wamkulu! 

13. lye ndi Yemwe 
akukuonetsani Zisonyezo Zake 






©ii 












*$wzi&&&#z 



&>. 



Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1008 



Yt *>l 



t * J\£> Sjj^ 



(zosonyeza Mphamvu Yake 
yoposa), ndipo akutsitsa madzi 
Kumwamba chifukwa cha inu kuti 
Abweretse zokupatsani umoyo; 
(Monga chakudya ndi zina). Koma 
Palibe amene akukumbukira 
kwenikweni Kupatula amene 
watembenukira (Kwa Mulungu). 

14. Choncho pembedzani 
Mulungu Pomuyeretsera 
mapemphero Ake Ngakhale 
(kumuyeretsera kwanu kwa 
Mapempheroko) kuwaipire okanira. 

15. lye Ngotukuka ulemerero, 
Mwini mpando Wachifumu; 
Amapereka chivumbulutso 
(Chake) mwa lamulo lake kwa 
Yemwe wamfuna mwa akapolo 
Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku 
Lokumana (anthu onse). 

16. Tsiku lomwe iwo 
adzaonekera Poyera (kwa 
Mulungu). Ndipo palibe 
Chilichonse chidzabisidwa kwa 
Mulungu (mzinthu zawo). (Ndipo 
Adzamva kufunsa koopsa ndi 
yankho Loopsa):"Kodi Ufumu 
ngwayani lero? Ngwa Mulungu 
mmodzi yekha, Wopambana, 
(woweruza mmene Akufunira kwa 
anthu Ake). 

17. Mzimu uliwonse lero, 
ulipidwa Zimene udachita; palibe 
chinyengo Lero (pochepetsa 



©4^ 















Siirat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1009 



Yi *>l 



i ♦ yiP dj_^*» 



mphoto kapena Kuonjeza 
chilango). Ndithu, Mulungu 
Ngwachangu (pa) chiwerengero 
Chake, (sichichedwa). 

18. Achenjeze (iwe, 
Mtumiki{SAW}) za tsiku Lomwe 
lili pafupi,(Kiyama) pamene 
Mitima idzakhala ku mmero 
(chifukwa Cha mantha oopsa) 
atadzadzidwa ndi Nkhawa. 
Wodzichitira chinyengo Sazakhala 
ndi bwenzi ngakhale Mpulumutsi 
womveredwa (Powateteza iwo). 

19. lye (Mulungu ) akudziwa 
Kuyang'ana kwa diso la chinyengo 
Ndi zimene zifuwa zikubisa 
(Mzobisika zonse). 

20. Ndipo Mulungu amaweruza 
mwa Chilungamo. Koma omwe 
Akuwapembedza kusiya Mulungu, 
Saweruza chilichonse (chifukwa 
cha Kufooka ndi kulephera 
kwawo). Ndithu, Mulungu yekha 
ndiye Wakumva Woona 
(chilichonse). 

21. Kodi sadayende padziko 
ndikuona Momwe mathero a anthu 
akale adalili? Adali opambana 
panyonga ndi Mzochitachita zawo 
zamdziko kuposa Iwo, (monga 
kumanga nyumba Zikuluzikulu). 
Koma Mulungu Adawaononga, 
psiti! chifukwa cha Machimo awo, 
ndipo adalibe Mtetezi ku chilango 
cha Mulungu. 



J> fit \Sf 9 . < .<* 9 S 












Surat 40. Ghafir Juzu 24 ioiO 1 t *>■' 



t • jte> djj-- 



22. Zimenezo nchifukwa 
Chakuti ankawadzera aneneri awo 
Ndi zizizwa zoonekera poyera, 
koma Adazikanira. Choncho 
Mulungu Adawaononga 
motheratu. lye Ngwanyonga 
zambiri, wolanga Mokhwima. 

23. Ndipo ndithu, tidamtuma 
Musa ndi zizizwa zathu Ndi 
zisonyezo zamphamvu Zoonekera 
poyera, 

24. Kwa Farawo ndi Haamana 
ndi Kaaruna. Ndipo adati, "(Uyu) 
ndi Wamatsenga, wabodza." 

25. Pamene (Musa) adawadzera 
ndi Choona chochokera kwa Ife, 
(Farawo pamodzi ndi omtsatira) 
adati: "Iphani ana achimuna a 
okhulupirira Pamodzi ndi iye; 
ndipo siyani ana Awo 
achikazi."Koma ndale za okanira 
Sizakanthu, nzotaika. 

26. Ndipo Farawo adati: 
"Ndilekeni Ndimuphe Musa; 
ampemphe Mbuye Wakeyo (kuti 
ampulumutse kwa ine)' Ine 
ndikuopera kuti angasinthe 
Chipembedzo chanu, Kapena 
kufalitsa Chisokonezo padziko." 

27. Ndipo Musa adati (kwa 
Farawo Pamodzi ndi anthu ake): 
"Ine Ndadzitchinjiriza ndi Mbuye 
wanga Amenenso ali Mbuye wanu 
(ku Chiwembu) chochokera kwa 












' Vv? -.f^' t?'•» u, ' f C—^""' 



Surat 40. Ghafir Juzu 24 



1011 tt*>» 



£ • J\* 0jj-» 



aliyense Wodzikweza, 
wosakhulupirira za tsiku La 
chiwerengero. 

28. Munthu wokhulupirira, 
wochokera Kubanja la Farawo 
yemwe adali kubisa Chikhulupiriro 
chake, adawalankhula (Anthu ake): 
"Kodi muphe Munthu chifukwa 
chakuti iye akunena Kuti, 'Mbuye 
wanga ndi Mulungu,' 
Chikhalirecho wakubweretserani 
Zisonyezo zoonekera poyera, 
zochokera Kwa Mbuye wanu? 
Ndipo ngati ali wabodza 
Pazomwe akunena ndiye kuti 
Kuipa kwa bodzalo kum'bwerera 
yekha. Koma ngati ali woona 
(pazomwe Akukulonjezani), ndiye 
kuti gawo lina La chilango 
chomwe akukulonjezani 
Likupezani; ndithu, Mulungu 
saongola Munthu wopyola malire, 
wabodza la Mkunkhuniza! 

29. E, inu anthu anga! Ufumu 
walero Ngwanu; mwagonjetsa 
dziko (la Iguputo). Ndani amene 
Angatipulumutse ku chilango cha 
Mulungu ngati chitatidzera?" 
Farawo Adati: "Sindikukupatsani 
maganizo Koma okhawo ndi 
kuwaona (kuti ndi Abwino) 
ndiponso sindikukuwongolerani 
Koma kunjira yoongoka." 

30. Ndipo munthu wokhulupirira 
uja Adanena: "E, inu anthu anga! 



e£*SM <3?tJ£* <3Kttfj 






6©3u»^5^Ji; 



Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1012 



Yi frjJUi 



£ * yip Sjj-- 



Ine Ndikukuoperani (za tsiku la 
masautso) Monga tsiku la magulu 
omwe (Adaukira aneneri awo). 

31. "Monga chikhalidwe cha 
Anthu a Nuhi, Adi, Samudi ndi 
Anthu omwe adadza Pambuyo 
pawo. Koma Mulungu Safuna 
kupondereza akapolo Ake. 

32. Ndiponso anthu anga! Ine 
ndikukuoperani Tsiku la kuitanana 
(anthu), 

33. Tsiku limene m'dzathawa 
ndi Kutembenuza misana yanu; 
pomwe Sim'dzakhala ndi mtetezi 
ku chilango Cha Mulungu; ndipo 
amene Mulungu Wamulekerera 
kusokera (chifukwa cha Zochita 
zake zoipa), ndiye kuti sangapeze 
Muongoli. 

34. Ndithu, adakudzerani kale 
Yusufu Ndi zisonyezo zoonekera 
poyera (Musa asadadze). Koma 
simudaleke Kuzikaikira zimene 
adadza nazo kwa Inu, kufikira 
pamene adamwalira, Mudati: 
"Mulungu sadzatumiza Mneneri 
wina pambuyo pake." Motero 
Mulungu amamulekerera kusokera 
Yemwe ali opyola malire, 
wokaikira Kwambiri. 

35. (Ali ngati awo) amene 
akutsutsana za Zisonyezo za 
Mulungu popanda Umboni 
uliwonse umene wawadzera. 



S9' 99. 9<' KX'<*9?\ 9<»\ * 









Surat 40. Ghafir Juzu 24 | 1013 | Y £ *>i 



£ * yip 5jj-- 



(Kutsutsa zisonyezo za Mulungu) 
Nchokwiitsa Mulungu kwakukulu 
ndi Kwa amene akhulupirira (mwa 
Mulungu). Momwemo ndi momwe 
Mulungu amadindira pamtima wa 
Aliyense wodzikuza, 
wodzitukumula." 

36. Ndipo Farawo adati: "E, iwe 
Haamana! Ndimangire Chipilala 
kuti ndikafike Kunjira, 

37. Njira za kumwamba kuti 
Ndikamuone Mulungu wa Musa. 
Koma ndithu, ine ndikudziwa Kuti 
ameneyu ngonama." Umo ndi 
momwe zochita zoipa za Farawo 
zidakongoletsedwera kwa iye, 
Ndipo adatsekeretsedwa ku njira 
yoona Ndipo chiwembu cha 
Farawo Sichakanthu, koma 
choonongeka. 

38. Ndipo uja wokhulupirira 
adati: "E, Inu anthu anga! 
Nditsatireni; Ndikuongolerani 
Kunjira yoongoka. 

39. E, inu anthu anga! Ndithu, 
Moyo wa padziko lapansi 
Ndichisangalalo (chakutha). 
Ndithu, tsiku lomaliza Ndiye 
nyumba yokhalamo muyaya. 

40. Amene akuchita choipa 
Sadzalipidwa chinachake Koma 
chofanana ndi chomwe Adachita. 
Ndipo yemwe Akuchita zabwino, 
mwamuna kapena Mkazi, uku iye 









A 



'^^U^iCr-'t &$3& 



$£*• -»• ' 






Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1014 



Tt *jir\ 



i * j31p 3jj~- 



ali okhulupirira, iwowo Adzalowa 
ku minda ya mtendere. 
Adzapatsidwa zopatsidwa 
Mmenemo zopanda chiwerengero. 

41. E, inu anthu anga! Chifukwa 
ninji, ine ndikukuitanirani Ku 
chipulumutso ndipo Inu 
mukundiitanira kumoto. 

42. Mukundiitanira kuti 
ndimkane Mulungu, ndimphatikize 
ndi milungu Yonama yomwe ine 
sindikuidziwa, Pomwe ine 
ndikukuitanirani kwa Mwini 
mphamvu zoposa; Wokhululuka 
kwambiri. 

43. Palibe chikaiko, ndithu, 
Mukundiitanira kuti 
ndiwapembedze Omwe alibe 
kuitana kulikonse pano Padziko 
lapansi ngakhale tsiku Lomaliza. 
Ndipo kobwerera kwathu Nkwa 
Mulungu basi. Ndipo, wopyola 
Malire (a Mulungu) iwowo ndiwo 
anthu Akumoto. 

44. Choncho posachedwa, 
Mudzakumbukira zimene 
Ndikukuuzanizi. Ndipo ine 
Ndikutula zinthu zanga Kwa 
Mulungu, ndithu, Mulungu akuona 
za anthu Ake." 

45. Choncho Mulungu 
Adam'teteza ku zoipa zomwe 
Adam'tchera. Ndipo chilango 



e^AWS 















Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1015 



ti *>» 



t * j3lP 5jj-» 



Choipa chidawazungulira anthu a 
Farawo (pamodzi ndi iye mwini.) 

46. Zilango za kumoto 
zikusonyezedwa Kwa iwo mmawa 
ndi madzulo. Ndipo Tsiku lomwe 
Kiyama idzapezeka, 
(Kudzanenedwa): "Alowetseni 
anthu a Farawo ku chilango cha 
ukali kwambiri (Choposa chomwe 
Adalandira mmanda mwawo)." 

47. Ndipo (akumbutse) pamene 
Azidzatsutsanam'moto! Pamene 
ofooka (Amene amatsatira) 
adzanena kwa Omwe adali 
kudzikweza: "Ndithu, ife Tidali 
otsatira anu; kodi simungathe 
Kutichotsera gawo lina la Chilango 
cha moto?" 

48. Awo amene adadzikweza 
adzati: "Ife Tonse tili muno. 
Ndithu, Mulungu Waweruza kale 
pakati pa anthu Ake. (Choncho 
palibe chilichonse chimene 
Tingaphulepo)." 

49. Ndipo akumoto 
adzalankhula kwa (Angelo) 
olondera Jahannama: 
"Tampempheni Mbuye wanu, 
Atipeputsire chilangochi Tsiku 
limodzi." 

50. (Alonda aja) adzati: "Kodi 
Sadakudzereni aneneri anu ndi 
Umboni oonekera poyera?" Iwo 
Adzati: "Inde, (adatidzera. Koma 






£)J*3 J£Mdt£«^J SIS 












Surat 40. Ghafir Juzu 24 



1016 I y i *>» 



i • yiP 5jj~- 



ife Tidanyoza)." (Ndipo) 
adzawauza: "Choncho pemphani 
nokha. Koma Pempho la okanira 
silili la kanthu, ndi Lotaika basi." 

51. Ndithu, Ife tikupulumutsa 
aneneri Athu Ndi amene 
akhulupirira pa moyo Wadziko 
lapansi ndi tsiku limene 
Zidzaimirira mboni (Kupereka 
umboni), 

52. Tsiku limene achinyengo 
Sadzawathandiza madandaulo 
awo, Ndipo matemberero 
adzakhala pa iwo, Ndipo pokhala 
pawo padzakhala Poipa kwambiri. 

53. Ndithu, Musa tidampatsa 
Chiongoko, ndipo Tidawasiira 
Buku ana a Israeli, 

54. (Lomwe lidali) chiongoko 
ndi Chikumbutso kwa eni nzeru. 

55. Choncho pirira, ndithu, 
Lonjezo la Mulungu ndi loona. 
Ndipo pempha chikhululuko Cha 
machimo ako, ndipo lemekeza 
Mbuye wako ndikumtamanda 
Madzulo ndi m'mawa. 

56. Ndithu, amene akutsutsana 
pa Zisonyezo za Mulungu popanda 
Umboni umene udawadzera, 
mmitima Mwawo mulibe 
chilichonse koma Kudzitukumula 
(ndikufuna ukulu), Koma saufikira. 
Dzitchinjirize mwa Mulungu: 
ndithu, lye Ngwakumva, Ngopenya. 



<M^]&*Mh£^ 









Surat 40. Ghafir Juzu 24 1017 I Y t ij±\ 



t * J\* 6jj*> 



57. Ndithu, kulenga kwa 
Thambo ndi nthaka nkwakukulu 
Kuposa kulenga kwa anthu. Koma 
anthu ambiri sakudziwa. 

58. Wakhungu ndi wopenya 
Ndiponso amene akhulupirira Ndi 
kumachita zabwino ndi Wochita 
zoipa (sali olingana). Zimene inu 
mukumbukira Nzochepa, ndithu! 

59. Ndithu, Kiyama idza; Ndipo 
za iyo palibe chikaiko. Koma 
anthu ambiri Sakhulupirira. 

60. Ndipo Mbuye wanu 
wanena: "Ndipempheni, 
ndikuyankhani; Koma amene 
akudzikweza ndi Mapemphero 
anga (posiya Kundipembedza), 
adzalowa ku Jahannama ali 
oyaluka." 

61. Mulungu ndi Yemwe 
adakupangirani Usiku kuti 
mupumule mmenemo, ndi Usana 
kukhala wounika (kuti muthe 
Kuchita ntchito zanu). Ndithu, 
Mulungu ndi Mwini Kupereka 
ufulu kwa anthu. Koma anthu 
ambiri sathokoza. 

62. Iyeyo ndiye Mulungu, 
Mbuye wanu; Mlengi wa 
chilichonse palibe wina 
Wopembedzedwa mwa Choona, 
koma Iye.Nanga Kodi 
mukutembenuzidwa chotani 
(Kuchoka ku zoona)! 






©WJ&*>)) 



©<££ 



• ^•X ,9% J 9S' 









Surat 40. Ghafir Juzu 24 | 1Q18 | Y t *> 



i • j31p ojj-j 



63. Momwemo ndi mmene 
Adatembenuziridwa Amene adali 
kutsutsa Zisonyezo za Mulungu. 

64. Mulungu ndi Amene 
adakupangirani Nthaka kukhala 
pamalo anu okhalapo, Ndi thambo 
kukhala ngati denga (Losagwa); 
ndipo adakujambulani 
Maonekedwe ndikukongoletsa 
Maonekedwe anu; ndipo 
adakupatsani Zinthu zabwino. 
Ameneyo ndiye Mulungu, Mbuye 
wanu. Choncho walemekezeka 
Mulungu, Mbuye wa zolengedwa." 

65. lye Ngwamoyo Wamuyaya; 
palibe Wopembedzedwa wina, 
koma lye. Choncho mpembedzeni 
momuyeretsera Chipembedzo. 
(Musapembedze Milungu ina 
mophatikiza ndi lye). 
Kuyamikidwa konse nkwa 
Mulungu, Mbuye wa zolengedwa. 

66. Nena: "Ine ndaletsedwa 
kupembedza Amene 
mukuwapembedza kusiya 
Mulungu, pamene zidandidzera 
Zisonyezo zoonekera kuchokera 
kwa Mbuye wanga; ndipo 
ndalamulidwa Kugonjera Mbuye 
Wa zolengedwa zonse." 

67. lye ndi Amene 
adakulengani kuchokera Ku dothi, 
kenako kuchokera kudontho La 
umuna, kenako kuchokera 






3* 












Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1019 



T£ *&\ 



t • jSIp Sjj— » 



mmagazi; Kenako 
ndikukutulutsani muli khanda; 
ndipo kenako (adakusiyani) kuti 
Mufike nthawi yanyonga zanu. 
Ndipo Kenako (adakulekani) kuti 
mukhale Nkhalamba. Ndipo ena a 
inu Amapatsidwa imfa asadaifike 
(Nthawi ya ukalamba) nkuti 
muifikire Nthawi imene yaikidwa; 
(Zoterezi nkuti inu) mukhale ndi 
nzeru. 

68. lye ndi Yemwe amapereka 
moyo ndi Kupereka imfa; ndipo 
akafuna kuchita Chinthu ndithu, 
amanenakwa Chinthucho: 
"Chitika," ndipo Chimachitika. 

69. Kodi sukuona amene 
Akutsutsana za zisonyezo za 
Mulungu? Kodi nchotani 
Akutembenuzidwa (Kusiya 
choonadi?) 

70- Amene alitsutsa Buku ndi 
zomwe Tidawatuma nazo atumiki 
athu; Koma posachedwa Adziwa, 

71. Pamene magoli ali 
m'makosi Mwawo, ndi unyolo Uli 
(mmiyendo) akukokedwa, 

72. M'madzi otentha, Kenako 
m'moto Akuotchedwa, 

73. Kenako adzauzidwa: "Hi 
kuti (Milungu) imene Mudali 
kuiphatikidza (Ndi Mulungu), 












®&j*J&i<j\ 









Sural 40. Ghafir 



Juzu 24 



1020 I 1 i *&\ 



t • j3lP 3j^» 



74. Mmalo mopembedza 
Mulungu?" Adzanena: "Yatisowa: 
koma chiyambire Kale sitidali 
kupembedza chilichonse (Kupatula 
Inu)." Umo ndi momwe Mulungu 
akuwalekerera kusokera Okanira. 

75. "Izi, (zimene zakupezani ku 
Moto kuno), nchifukwa Chakuti 
mudali kudzikweza Padziko 
mosayenera. Ndiponso Chifukwa 
chakuti mudali kunyada. 

76. Lowani m'makomo a 
Jahannama; mukhala Mmenemo 
muyaya. Taonani kuipa Malo a 
odzikweza!" 

77. Pirira, ndithu, lonjezo la 
Mulungu ndiloona. Mwina 
Tikusonyeza zina mwa Zomwe 
tawalonjeza, kapena Tikupatsa imfa 
(usadazione. Basi, Palibe chikaiko, 
zichitika chifukwa Chakuti onse) 
adzabwezedwa kwa Ife. 

78. Ndithu, tidawatuma atumiki 
patsogolo Pako; ena mwa iwo 
tidakusimbira (Nkhani zawo ndi 
maina awo). Ena mwa iwo 
sitidakusimbire. Sikudali kotheka 
kwa Mtumiki Aliyense kudzetsa 
chozizwitsa Mwa yekha, koma 
mchifuniro Cha Mulungu. Ndipo 
lamulo la Mulungu likadzadza, 
Kudzaweruzidwa mwa choonadi. 
Ndipo ochita zachabe Panthawi 
imeneyo Adzataika; (adzaluza). 






H&9S? '\>\ 9 - 9 * } i\}*Y\' 9 \ 9 






Surat 40. Ghafir 



Juzu 24 



1021 



Yi *>i 



i ♦ yip *jj~* 



79. Mulungu ndi Yemwe 
Wakupangirani nyama kuti 
Mudzizikwera zina mwa izo.Ndipo 
zina mwa izo kuti muzidya; 

80. Ndipo mmenemo muli 
Zokuthandizani zambiri; Ndipo 
kupyolera mzimenezo Mukupeza 
zofuna za mitima yanu; Pa izo, ndi 
pa zombo, Mukunyamulidwa. 

81. Ndipo (lye nthawi zonse) 
Akukuonetsani zisonyezo Za 
chisomo Chake. Kodi ndi Ziti 
m'zisonyezo za Mulungu zimene 
Mukuzikana (kuti sizake)? 

82. Kodi sadayende padziko 
ndikuona Momwe adalili mathero 
a omwe adali Patsogolo pawo? 
Adali ochuluka Kwambiri kuposa 
iwo; ndiponso Adali anyonga 
kwambiri ndi Ochulukitsa 
zomangamanga mdziko. Koma 
sizidawathandize zimene adali 
Kuchita. 

83. Koma pamene atumiki awo 
Adawadzera ndi zisonyezo 
Zoonekera, adakondwera ndi 
Nzeru zomwe adali nazo, (ndipo 
Sadalabadire zomwe atumiki 
adadza Nazo). Choncho 
zidawazinga zimene Adali 
kuzichitira chipongwe. 

84. Ndipo pamene adachiona 
Chilango chathu, adanena (kuti): 
"Takhulupirira mwa Mulungu 






®&$#<&$&&Af& 



9s 









t&$$^®®3(m 



Surat 40. Ghafir Juzu 24 1022 * $ *j*-i 



t • ^dip *jj**' 



Mmodzi, ndipo tikuzikana Zimene 
tidali kumphatikiza Nazo." 

85. Koma chikhulupiriro chawo 
sichidali Chowathandiza panthawi 
imeneyo, Pomwe adali atachiona 
kale chilango Chathu.Ichi ndi 
chizolowezi cha Mulungu chomwe 
chidapita pa anthu Ake (onse kuti 
chilango chikadza, Kulapa 
sikuvomerezedwa). Choncho 
Pamenepo, okanira adaluza. 







Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1023 



1 1 *j£-1 i > cJLad Sjj-» 




Surayi yayamba ndi malembo awiri monga njira ya Qur'an 
m' Surah zambiri. Ndipo nkhani yaikulu msurayi ndi kufotokoza 
za ulemerero wa Qur'an ndi zomwe zili m'kati mwake monga 
kupereka uthenga wabwino kwa anthu ochita zabwino, ndi 
kuwachenjeza anthu ochita zoipa. Ndiponso yafotokoza za 
maganizo a Amushirikina pa Qur'an, monga kuinyoza ndi 
kuuthira nkhondo ulaliki wake. Ndi momwe Mtumiki (SAW) 
adalimbikirira kuwalalikira iwo powauza kuti: "Ndithu, ine 
ndine munthu monga inu. Kusiyana kwanga ndi inu nkwakuti 
kwavumbulutsidwa mawu kwa ine oti: "Ndithu, Mulungu wanu 
ndi Mulungu Mmodzi yekha. Lungamani kwa lye, ndipo 
mpempheni chikhululuko." 

Surayi ikukumbutsanso Amushirikina za zisonyezo za Chauta 
zolangiza mphamvu Zake zoposa, monga kalengedwe ka 
thambo, nthaka, ndi zina zotere. Kenako yaopseza za zomwe 
zidawapeza amibadwo yapafupi ndi midzi yawo, monga Adi ndi 
Samud. Ndipo ikuwakumbutsanso za tsiku lomaliza; tsiku 
limene makutu awo, maso awo ndi khungu lawo zidzawaikire 
umboni pa zoipa zimene adali kuchita. Ndipo ikufotokozanso za 
mkangano umene udzakhalepo pakati pa iwo ndi ziwalo zawo. 
Ndipo yapitirira ndikufotokoza kuti otsatira adzapempha Chauta 
kuti atsogoleri awo omwe adali kuwasokeretsa asonyezedwe 
kwa iwo kuti athane nawo powaponda ndi mapazi awo. 

Monga mwa njira ya Qur'an, ikafotokoza za anthu oipa 
imafotokozanso za anthu abwino, chonchonso Surah iyi 
yafotokozanso za anthu abwino omwe amanena kuti: "Mbuye 
wathu ndi Mulungu." Ndipo kenako ndikupitiriza kuchita 
zolungama. Anthu otere alonjezedwa mtendere wamuyaya. 
Ndipo yafotokozanso kuti choipa ndi chabwino sizilingana. 

Kenako Surayi yadzidzimutsa maso a anthu kuti ayang'ane 
zisonyezo za Mphamvu ya Mulungu yomwe ikusonyeza kuti 
Chauta adzatha kupatsa moyo akufa. Ndipo yabwerezanso 



Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1024 



V t i£r\ t ^ cJUa3 dj^-» 



kachiwiri kuopseza anthu opotola zisonyezo za Mulungu 
ndikuwauza kuti iwo sangabisike ndi Chauta ngakhale pang'ono. 
Ndiponso kuti Buku ili la Qur'an palibe chimene chingapunguke 
Mmawu ake, kapena kuonjezeka. Qur'aniyi ndi chivumbulutso 
chochokera kwa Wanzeru ndi Wotamandidwa. Ndipo Uthenga 
wa Muhammad (SAW) suthenga wachilendo. Koma ukulingana 
ndi uthenga umene aneneri a kale adadza nawo. 

Ndipo Surayi ikufotokozanso za chikhalidwe cha munthu 
ponena kuti akadalitsidwa ndi madalitso ambiri amanyoza choona. 
Koma choipa chikamkhudza amapempha Chauta pafupipafupi. 

Pomaliza Surayi yanenetsa za mfundo ziwiri zomwe zili 
zofunika kwabasi kuposa zolinga zake zonse zimene 
yasonkhanitsa. Choyamba ndi kudziwitsa za Qur'an kuti 
chimenechi ndi choona; mulibe chokaikitsa chilichonse monga 
momwe Mulungu wanenera kuti: "Tiwasonyeza zisonyezo zathu 
mbali zosiyanasiyana ndi mmatupi mwawo kufikira zionekere 
poyera kwa iwo kuti Qur'an ndi yoona." 

Chachiwiri ndikuti palibe chilichonse kwa osakhulupirira 
chimene chawachititsa kuti asakhulupirire, koma ndi mtsutso 
wawo pa zakuuka kwa akufa. 




Siirat 41. Fussilat Juzu 24 



1025 



tt frj*-i 



£ > cJL^ ^jj-*» 



Surat Fussilat XLI 




M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim: 

2. (Qur'an iyi) 
ndichivumbulutso Chochokera 
kwa Wachifundo chambiri, 
Wachisoni; 

3. (Hi) ndi Buku lomwe ma aya 
ake Afotokozedwa (bwino 
pokhudza Malamulo a zamdziko 
ndi tsiku Lomaliza); 
Chowerengedwa (chimene 
Chavumbulutsidwa) 
m'chilankhulo cha Chiarabu kwa 
anthu ozindikira (Tsatanetsatane 
wa malamulo ake); 

4. Likunena nkhani yabwino 
(kwa ochita Zabwino) ndi 
kuchenjeza (anthu ochita Zoipa); 
koma ambiri a iwo (Akuraish) 
Ainyoza kotero kuti sakumva; 
(kumva Kothandizidwa nalo ndi 
kulilingalira). 

5. Ndipo akunena (kuti): 
"Mitima yathu (Yaphimbidwa) 
m'zivindikiro, ku Zomwe 
ukutiitanirazo, ndipo m'makutu 
Mwathu muli kulemera kwa 
ugonthi; Choncho pakati pathu ndi 
pakati pa iwe Pali chotsekereza 



o^l^JII^ 















Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1026 



Tt *>i 



t\ 



dj^ 



(chotchinga); tero Chita (zakozo); 
nafe tichita (zathu; Aliyense wa ife 
asalowerere za Mnzake)". 

6. Nena: "Ndithu, palibe 
chikaiko, ine ndi Munthu monga 
inu; Kukuvumbulutsidwa kwa ine 
(Kuchokera kwa Mulungu) kuti 
ndithu Mulungu wanu ndi 
Mulungu Mmodzi; Choncho 
lungamani kwa lye ndipo 
Mpempheni chikhululuko (pa 
zimene Mwakhala 
mukumchimwira)" Ndipo 
kuonongeka Kwakukulu kuli pa 
ophatikiza (Mulungu ndi zinthu 
zina), 

7. Amene sapereka Chopereka 
(zakaat), ndi omwe Akukanira za 
tsiku lomaliza. 

8. Ndithu, amene akhulupirira 
ndi Kumachita zabwino, pa iwo 
padzakhala Malipiro osadukiza 
(osatha). 

9. Nena: "Kodi inu 
mukumkanira Yemwe adalenga 
nthaka Mmasiku awiri (okha)? 
Ndipo mukumpangira Milungu 
(ina)? Iyeyo ndiye Mbuye Wa 
zolengedwa zonse. 

10. Ndipo adaika pamenepo 
mapiri Ataliatali pamwamba pake, 
ndi Kudalitsapo (ndi madzi, 
mmera, ndi Ziweto), ndipo adayesa 
mmenemo Zakudya zake (za 






^AJVJtJ-J&^U 






Surat 41. Fussilat Juzu 24 fl027 * * *> 



n 



°j>- 



okhala pa nthakapo; Zimenezi 
adadzichita) mmasiku anayi; (Izi) 
nzokwanira kwa ofunsa 
(Zakalengedwe ka nthaka ndi 
Zamkati mwake). 

11. Kenako adaganiza zolenga 
thambo Pomwe ilo lidali utsi. 
Ndipo adati Kwa ilo ndi nthaka: 
"Idzani, mofuna Kapena 
mosafuna, (Tsatirani lamulo 
langa)." Izo zidayankha Kuti: 
"Tadza momvera." 

12. Choncho adakwaniritsa 
kulenga Thambo zisanu ndi ziwiri 
mmasiku Awiri, ndipo thambo 
lililonse Adalidziwitsa ntchito 
yake (polilamula Zochita zake). 
Ndipo tidakongoletsa Thambo 
lapafupi (ndi inu) ndi nyenyezi 
(Zounikira dziko lapansi), 
ndiponso kuti Zizilondera 
kumwamba (kuti ziwanda 
Zisamapite kukamvera za 
kumwamba). Uwu ndi muyeso wa 
Mwini Mphamvu, Wodziwa 
kwambiri. 

13. Koma ngati anyozera 
(Kukhulupirira), nena: 
"Ndikukuchenjezani za Chilango 
monga chilango Cha Adi ndi 
Samud." 

14. Pamene aneneri adawadzera 
patsogolo Pawo ndi pambuyo 
pawo (Ndikuwauza): 












Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1028 



Ti *>■» 



t ^ cJ L^ <>jj~> 



"Musapembedze (Milungu ina), 
koma Mulungu (Mmodzi)," Adati: 
"Mbuye Wathu akadafuna, 
akadatsitsa Angelo (Kudzatilalikira, 
osati anthu monga Inu). Ndithu, ife 
tikuzikana Zimene mwatumidwa 
nazozo." 

15. Tsono Adi adadzikweza 
padziko Mosayenera, ndipo adati: 
"Ndani wamphamvu kuposa ife?" 
Kodi saona kuti Mulungu Yemwe 
adawalenga ndi mwini Mphamvu 
zambiri kuposa iwo? Koma 
adapitiriza kukanira zozizwitsa 
Zathu. 

16. Choncho tidawatumizira 
mphepo ya Mkuntho yozizira 
kwabasi mmasiku Amatsoka, kuti 
tiwalawitse chilango 
Chowasambula pamoyo wa padziko 
Lapansi; ndipo chilango cha tsiku 
Lomaliza ndi choyalutsa kwambiri; 
Ndipo iwo sadzapulumutsidwa. 

17. Naonso Asamudu 
tidawasonyeza (njira Yabwino ndi 
njira yoipa), ndipo Adakonda ndi 
kusankha kusokera Kusiya 
chiongoko; ndipo udawapeza 
Nkuwe wa chilango choyalutsa 
Chifukwa cha machimo Amene 
adali kuchita. 

18. Koma tidawapulumutsa (Ku 
chilango chimenechi) Amene 
adakhulupirira ndi Kumamuopa 
Mulungu. 









%&3 






®u%fMp\&$mj 



Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1029 



Ti *jfcl 



i> 



•jj*. 



19. Ndipo (akumbutse, iwe 
Mtumiki), tsiku Lomwe adani a 
Mulungu Adzasonkhanitsidwa 
kunka nawo ku Moto, uku 
akukusidwa (onse, oyamba Ndi 
omalizira), 

20. Kufikira pomwe adzaufikira 
(moto); Makutu awo ndi maso awo 
Ndi khungu lawo zidzawachitira 
Umboni pa zomwe adali Kuchita 
(padziko lapansi). 

21. Ndipo adzanena (adani a 
Mulungu) ku Makungu awo: 
"Bwanji mukutiperekera Umboni 
woipa?" Zidzati: "Mulungu 
Watilankhulitsa: Amene 
amalankhulitsa Chilichonse; ndipo 
lye ndi Amene Adakulengani 
(mkulenga) koyamba (Pomwe 
simudali kanthu), ndiponso kwa 
lye yekha ndiko mudzabwezedwa. 

22. Simudathe kubisa (ntchito 
zanu zoipa) Ku ziwalo zanu 
poopera kuti kumva Kwanu ndi 
kuyang'ana kwanu ndi Makungu 
anu zingakuperekereni Umboni 
woipa! Koma mudali kuganiza 
Kuti Mulungu sadziwa zambiri 
zomwe Mukuzichita (mobisa). 

23. Ndipo amenewo ndi 
maganizo anu Omwe mudali 
kumganizira (nawo) Mbuye wanu 
adakuonongani, ndipo (Lero tsiku 
la Kiyama) muli m'gulu la Otaika." 









if 


















Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1030 



Tt fr>i 



i> 



dj^ 



24. Choncho ngakhale atapirira 
(ku Zopweteka zawo), moto ndiwo 
Mabwerero awo ndi kokhazikika 
kwawo Kwa muyaya.Ngati 
atapempha chiyanjo Cha Mulungu 
pa iwo, iwo sadzakhala M'gulu la 
oyanjidwa. 

25. Ndipo tidawakonzera iwo 
abwenzi Oipa (padziko lapansi), 
choncho Adawakometsera 
zamtsogolo mwawo Ndi za 
pambuyo pawo ndipo liwu la 
Chilango lidatsimikizika pa iwo 
pamodzi Ndi mibadwo yomwe 
idapita kale ya Ziwanda ndi anthu, 
ndithu iwo adali otaika. 

26. Akunena okanira (kuuzana 
okhaokha): "Musamvetsere Qur'an 
iyi, koma Sokoserani pomwe 
ikuwerengedwa (kuti Asaimvere 
aliyense) kuti mwina Mupambane." 

27. Ndithu tiwalawitsa amene 
Akanira chilango choopsa (Pa 
zochita zawo zoipa,makamaka 
Pakuithira Qur'an nkhondo), 
Ndipo ndithu tiwalipira malipiro 
oipa Chifukwa cha zoipa zomwe 
adali kuzichita. 

28. Imeneyo ndi mphoto 
yoyenera ya adani a Mulungu, 
yomwe ndi moto. Mmenemo 
Adzakhala muyaya. Imeneyi ndi 
mphoto Ya zimene adali 
kuzikanira M'zisonyezo Zathu. 


















Surat 41. Fussilat Juzu 24 I 1031 1 1 *j*-i 



i\ 



dj^ 



29. Ndipo okanira adzanena (ali 
mkati mwa Mo to): "E, Mbuye 
wathu! Tisonyezeni (Magulu awiri) 
amene adatisokeretsa. Ochokera 
m'ziwanda ndi anthu kuti Tiwaike 
pansi pa mapazi athu, kuti Akhale 
apansi (mu ulemerero ndi Malo)." 

30. Ndithu amene anena (kuti): 
"Mbuye Wathu ndi Mulungu," 
(povomereza Umodzi Wake), 
kenako nkupitiriza Kulungama pa 
malamulo Ake, angelo 
Amawatsikira iwo nthawi yakufa 
(uku Akuti): "Musaope (pazomwe 
Mukumane nazo). Ndipo 
Musadandaule (pazomwe 
mwazisiya). Ndipo sangalalani ndi 
munda Wamtendere umene 
mudalonjezedwa (Kupyolera 
mmalirime a aneneri). 

31. (Angelo amanena kwa iwo): 
"Ife ndi Athangati anu pamoyo wa 
padziko Lapansi (pokulimbikitsani 
panjira Yolungama), ndi tsiku 
lomaliza (Pokupempherani 
chipulumutso kwa Mulungu); inu 
mukapeza kumeneko Chilichonse 
chomwe mitima yanu Ikafune 
(zokoma ndi zabwino); ndipo, 
Mukapeza mmenemo chilichonse 
Chomwe mukachilakelake. 

32. (Limeneli ndi) phwando 
Lochokera kwa (Mbuye) 
Wokhululuka Kwambiri, 
Wachisoni." 



£*' 















Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1032 



tt *>» 



i> 



dj^ 



33. Kodi ndani yemwe ali ndi 
zonena Zabwino kuposa yemwe 
akuitanira kwa Mulungu (ndi 
kumumvera), Ndikuchita, 
(pamodzi ndi zimenezo), Zabwino 
uku akunena: "Ine Ndi mmodzi 
mwa ogonjera (malamulo a 
Mulungu)." 

34. Ndipo chabwino 
Sichingafanane ndi choipa. 
Chotsani choipa (ngati 
chitakufikani Kuchokera kwa 
mdani), ndi (chinthu) Chabwino; 
mapeto ake akhala kuti Yemwe 
padali chidani pakati pako ndi 
Pakati pake (akhala) ngati 
mthandizi Wodalirika. 

35. Ndipo palibe angapatsidwe 
zimenezi (Zochotsa choipa pochita 
chabwino) Kupatula amene apirira. 
Ndiponso sangapatsidwe zimenezi 
Kupatula mwini gawo la ubwino 
waukulu. 

36. Ndipo ngati satana 
atakusokoneza kuti Akuchotse ku 
zomwe walamulidwa, Pempha 
chitetezo kwa Mulungu. Ndithu, 
lye Ngwakumva zonse, Ngodziwa 
zonse; (adzakuteteza Kwa iye). 

37. Ndipo zina mwa zisonyezo 
Zake, Ndi usiku, usana, dzuwa ndi 
mwezi. Musalambire dzuwa 
ngakhale mwezi, Koma lambirani 
Mulungu (Mmodzi), Amene 


















Surat 41. Fussilat Juzu 24 



1033 



t£ *>1 



t> c 



*lf 



adazilenga ngati inu 
Mumpembedza moona. 

38. Koma ngati adzikweza 
(Amushirikina Ndi kusiya kutsatira 
lamulo lako, Usade nkhawa). 
Ndipo, amene ali Kwa Mbuye 
wako; (angelo), akulemekeza lye 
usana ndi usiku, ndipo iwo Satopa 
(ndi kutamanda Mulungu). 

39. Zina mwa zisonyezo Zake 
(Zoposa), ndithu, iwe umaona 
nthaka Hi youma; koma tikatsitsa 
madzi pa iyo Imagwedezeka ndi 
kufufuma; ndithu, Amene 
waiukitsa nthaka itauma, 
Ngoyenera kuukitsa akufa. lye 
Ngwamphamvu zoposa Pa 
chilichonse. 

40. Ndithu, amene akupotoza 
choonadi Mzisonyezo Zathu 
sangabisike kwa Ife. (Ndipo 
tidzawalipira zimene akuyenerana 
Nazo). Kodi wabwino ndi uti, 
yemwe Adzaponyedwa ku moto, 
kapena Yemwe adzadza pa tsiku la 
chiweruzo Uku ali wokhazikika 
mtima? Chitani Zimene mukufuna; 
ndithu, lye Ngopenya chilichonse 
chimene Mukuchita. (Aliyense 
adzamulipira pa Zochita zake). 

41. Ndithu, amene atsutsa 
Qur'an Yolemekezeka ikawadzera 
(popanda Kulingalira, kwa iwo 
kudzakhala Chilango 


















Siirat 41. Fussilat Juzu 24 



1034 



tt t,jir\ 



£\ 



d J>-" 



chosasimbika). Ndipo ndithu, 
Limeneli ndi Buku lopambana 
(Chilichonse cholipinga). 

42. Siifikidwa ndi chonama 
patsogolo pake Ngakhale pambuyo 
pake. Ndi lovumbulutsidwa 
kuchokera kwa Wanzeru zakuya, 
Woyamikidwa Kwambiri 
(mzochita Zake). 

43. Palibe chimene chinenedwa 
kwa iwe (Mtumiki{SAW} 
kuchokera kwa adani Ako) koma 
chomwe chidanenedwa Kwa 
aneneri akale (kuchokera kwa 
Adani awo). Ndipo Mbuye wako 
ndi Mwini chikhululuko chambiri 
(kwa Amene walapa kwa lye), 
ndiponso Mwini chilango 
chowawa (kwa yemwe Wapitiriza 
mwano). 

44. Tikadaichita Qur'an iyi 
kukhala Mchilankhulo china osati 
Chiarabu, Akadanena: "Nchifukwa 
ninji ma Aya ake sadafotokozedwe 
bwino; Buku la chilankhulo 
chachilendo Olalikidwa nkukhala 
Mwarabu?" Nena (iwe 
Mtumiki): "Limeneli ndi 
Chiongoko ndi chochiritsa kwa 
Okhulupirira. Koma kwa amene 
Salikhulupirira (zili ngati kuti) 
mmakutu Mwawo muli ugonthi 
(chifukwa Cholinyoza).Umene 
ukuwachititsa khungu (Chifukwa 
choti saona chilichonse Mmenemo 









^%&mtit&&Ms 






Surat 41. Fussilat Juzu 25 



1035 



To *>i 



i\ 



°JJ*" 



chowapindulitsa) Iwo,okanirawo 
ali ngati akuitanidwa Ndi woitana 
kuchokera pamtunda Wapatali 
(kuti amkhulupirire)." 

45. Ndipo ndithu, tidampatsa 
Musa Buku (La Taurat.) Ndipo 
(anthu ake) adatsutsana Za ilo. 
Kukadapanda kutsogola liwu 
Lochokera kwa Mbuye wako (loti 
Adzachedwetsa chilango kwa 
okutsutsa) Kukadaweruzidwa 
pakati pawo (Powaononga). 
Ndithu, iwo ali M'chikaiko 
choikaikira iyo (Qur'an). 

46. Amene ati achite chabwino, 
Akudzichitira yekha; ndipo amene 
Akuipitsa (m'zochita zake), 
machimo Ake ali pa iye 

yekha. Mbuye wako sali 
Wopondereza anthu Ake (polanga 
wina Ndi tchimo la wina). 

47. Kudziwa kwa tsiku la 
Kiyama Kukubwezedwa kwa Iye 
(Mulungu;) Zipatso sizituluka 
m'mikoko yake ndipo Mkazi 
satenga pakati ndi kubereka 
Popanda Mulungu kudziwa. 
(Koma Amadziwa zonsezo 
bwinobwino). Ndipo (kumbukira) 
tsiku limene Mulungu 
Adzawaitane (ndi kuwafunsa kuti): 
"Ali kuti aphatikizi Anga aja 
(amene Mudali kuwapembedza 
kusiya Ine)?" Adzanena 
(modandaula): "Tikukudziwitsani, 












Siirat 41. Fussilat Juzu 25 



1036 



To frjJUi 



t> 



°J>- 



(E, Inu Mulungu)! Palibe aliyense 
mwa ife angaikire Umboni (kuti 
Inu muli ndi mnzanu)." 

48. Ndipo zomwe adali 
Kuzipembedza kale zidzawasowa. 
Ndipo adzatsimikiza kuti Alibe 
pothawira. 

49. Munthu satopa kupempha 
zabwino (Zam'dziko lapansi kwa 
Mbuye wake). Koma choipa 
chikamkhudza iye Amakhala 
wotaya mtima Kwambiri. 

50. Ndipo ndithu, tikamulawitsa 
chisomo Chathu atapeza mavuto 
kwambiri amene Adamkhudza, 
ndithu, amanena, (Monyada): "Izi 
nzangazanga. (Ndazipeza 
chifukwa Cha khama langa ndi 
nzeru zanga): Ndipo za tsiku 
lomaliza Sindikhulupirira kuti 
lilipo. Ndipo ngati nditabwezedwa 
kwa Mbuye wanga, ndiye kuti ine 
Ndidzakhala nazo zabwino kwa 
Iye." Choncho tidzawauza omwe 
adakanira Zimene adachita, ndipo 
tidzawalawitsa Chilango 
chokhwima (chosanjikana China 
pamwamba pa chinzake). 

51. Ndipo munthu tikam'dalitsa 
ndi chisomo Chathu, amanyoza ndi 
Kudziika kutali (ndi chipembedzo 
Chathu). Koma vuto likam'khudza 
Umuona uyo akuchulukitsa 
Maduwa (mapemphero). 












Surat 41. Fussilat Juzu 25 



1037 



To *>t 



i S cJUa3 5jj-»» 



52. Nena (kwa iwo, iwe 
Mtumiki): "Tandiuzani ngati 
(Qur'aniyi) ilidi Yochokera kwa 
Mulungu, kenako inu Nkuikanira; 
(nanga zingakhale bwanji?) Kodi 
ndiyani wosokera kwambiri 
Kuposa uyo amene ali mumtsutso 
Wakutali (ndi choona)?" 

53. Posachedwa tiwaonetsa, 
(awa okanira), Zisonyezo Zathu 
(zosonyeza kuona kwa Qur'an ndi 
iwe) kumbali zonse, Ndi mwa iwo 
eni kufikira zionekere kwa Iwo 
kuti chimene wadza nachochi 
Nchoona. Kodi Mbuye Wako 
siwokwanira kuti lye Akuona 
chilichonse? 

54. Chenjerani! Ndithu, awa ali 
m'chikaiko Za kukumana ndi 
Mbuye wawo. Ndithu, lye (Mbuye 
wawo) wachizungulira Chinthu 
chilichonse Mkudziwa Kwake. 













Surat 42. Ash-Shut a Juzu 25 I 1038 I ** *>' i T c^jj-^' *j>- 




SURAT ASH-SHURA XLII ^^S|| 

— __— _ - — -^ .^^Q^^^f 

Surayi yayamba ndi kunenetsa mwandithundithu kuti Qur'an 
ndi chivumbulutso chochokera kwa Mulungu potsutsa zimene 
ankainenera okanira. Ndipo ikulimbitsa kumtonthoza Mtumiki 
(SAW) kumavuto omwe amapezana nawo kuchokera kwa 
anthu otsutsa. 

Kenako Surayi yalimbikitsa za Mphamvu za Mulungu ndi 
ukulu Wake ndiponso ufumu Wake, lye amene adaivumbulutsa. 

Koma anthu ena adaikanira ngakhale zisonyezo zake zoti 
njochokera kwa Mulungu zili zoonekera. Ndipo yafotokoza 
zakusiyana kwawo popeza choonacho. 

Surayi yanenanso za kuphatikiza Chauta ndi mafano zomwe 
Amushirikina amachita ndi kutsutsana kwawo pa choona 
ndikufuna kuti Kiyama idze mwachangu ponena 
mwachipongwe. 

Surayi yationgolera mmene tingawaitanire anthu ku dini 
(mpingo). Ndiponso yafotokoza zakukula kuleza mtima kwa 
Mulungu pa anthu Ake. 

Kenako surayi yachenjeza zakususuka ndi zamdziko 
ndikufotokoza za kuipa kwa chikhalidwe cha anthu okanira pa 
tsiku la Kiyama, ndiubwino wa chikhalidwe cha anthu 
okhulupirira. Ndipo yafotokozanso zoti Chauta amalandira 
kulapa kwa okhulupirira. Ndiponso kuti Mulungu amagawa 
riziki (chuma) pakati pa anthu mosiyanitsa: ena olemera, ena 
osauka kuti anthuwo asaononge dziko lapansi. 

Surayi yapitirira ndi kufotokoza zakukula kwa dalitso la 
mvula ndi zisonyezo zolangiza mphamvu za Mulungu padziko. 
Ndikuti mavuto am 'dziko lapansi amachitika chifukwa cha 
machimo. 

Kenako Surayi ikutiuza kuti tichite changu kuyankha kuitana 



Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 J 1039 I * * *&\ t T ^ jjiJi *j>- 



kwa Mulungu, moyo usanathe; imene ndi nthawi yopindulitsa 
pogwira ntchito zabwino. Ndipo yanka patsogolo kufotokoza za 
mphamvu ya Mulungu pompatsa ana achikazi kapena achimuna 
amene wamfuna. Kapena pompatsa ana achikazi pamodzi ndi 
achimuna ndi kumchita wina kukhala wosabereka. 

Ndipo potsirizira surayi yafotokoza mmene Mulungu 
amawalankhulira aneneri Ake. Kenako nkudzamaliza ndi 
kulongosola njira yoona yofunika kuitsata. 




Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 I 1040 I To^i it tfjjiJi *j>-> 



Surat Ash-Shura XLII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim, 

2. 'Ain-Sin-Qdf. 

3. Chomwecho 
akukuvumbulutsira iwe Ndi atumiki 
amene adadza kale, Mulungu 
Ngopambana Wanzeru zakuya. 

4. Zonse za kumwamba ndi 
pansi ndi za lye Yekha. Ndipo lye 
ndi Wotukuka, Wamkulu. 

5. (Chifukwa chakukula Kwake 
ndi Ulemerero Wake) mitambo 
Ikuyandikira kuphwasuka 
pamwamba Pa iyo.Ndipo angelo 
akulemekeza ndi Kutamanda 
Mbuye wawo, ndi kuwapemphera 
Chikhululuko amene ali padziko 
lapansi. Dziwani kuti ndithu, 
Mulungu Yekha ndiye 
Wokhululuka kwabasi, Wachisoni. 

6. Ndipo awo amene 
adzipangira athandizi (A mafano) 
kusiya Mulungu, Mulungu Ndi 
wofondera (zocfrita) zawo; ndipo 
Iwe sikapitawo wawo (wosunga 
Zochita zawo). 

7. Chomwechonso (monga 
chilili Chivumbulutso 
chapoyerachi) Takuvumbulutsira 






Q^t^i^U, 



-£. 



($1 















Siirat 42. Ash-Shiira Juzu 25 I 1041 I Y o tj±-\ t Y tf jjiJi dj>- 



Qur'an m'Chiarabu (Popanda 
chikaiko) kuti uchenjeze (Eni) 
Likulu la mizinda (Makka) ndi 
amene Ali m'mbali mwake, 
ndikutinso uchenjeze (Anthu) za 
tsiku la msonkhano, lopanda 
Chikaiko. (Pa tsikulo anthu 
adzagawikana Mmagulu awiri): 
gulu Una ku Janna, ndipo Gulu lina 
kumoto. 

8. Ndipo akadafuna Mulungu 
Akadawachita iwo kukhala 
Mpingo umodzi; koma akulowetsa 
ku Chifundo Chake amene 
wamfuna Ndipo odzichitira okha 
chinyengo (Pokana Mulungu) 
adzakhala opanda Mtetezi kapena 
mthandizi. 

9. (Kapena adzichitira athandizi 
Ena kusiya lye (Mulungu;) 
kumachita Kuti Mulungu Yekha 
ndiye Mthandizi woona ndipo lye 
amaukitsa akufa. Ndipo lye ndi 
Wokhoza pa chilichonse. 

10. Ndipo chilichonse chimene 
mwasiyana Mmenemo 
(mchipembedzo: Za Kukhulupirira 
ndi kusakhulupirira) Chiweruzo 
Chake nkwa Mulungu; (Bwererani 
ku Buku la Mulungu ndi Hadith za 
mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi 
Mulungu, Mbuye wanga; Kwa lye 
Yekha ndatsamira, Ndipo kwa lye 
Yekha (ndiko) Ndikutembenukira. 



^m\^i^& 



9 <A 









t$9 C 



'V 






Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 I 1042 I t a *>i t T <j?jj-iJt «jj~- 



11. (lye ndi) Mlengi wa 
kumwamba ndi Pansi. 
Adakupangirani akazi Kuchokera 
mwa inu nomwe, Ndipo nazo 
ziweto mitundu Iwiri, (zazimuna 
ndi zazikazi. Choncho) 
akukuchulukitsani mmenemo 
(Mchikonzero Chake chanzeru) 
palibe Chilichonse chofanana ndi 
lye. lye Ndi Wakumva zonse 
ndiponso Woona Zonse. 

12. Makiyi a kumwamba ndi 
pansi ndi Ake. Amamchulukitsira 
riziki amene wamfuna Ndipo 
amamchepetsera amene Wamfuna. 
Ndithu, lye Ngodziwa 
Chilichonse(pochiika pamalo 
Oyenerana nacho). 

13. Wakhazikitsa kwa inu 
chipembedzo Chonga chomwe 
adam'langiza Nuhi. Ndipo 
chimene takuvumbulutsira iwe 
Ndi chimenenso tidavumbulutsira 
Ibrahim, Musa, ndi Isa kuti: 
Mulimbike Chipembedzo 
(potsatira Malamulo) ndikuti 
musalekane pa Chipembedzo. 
Koma ndizovuta kwa Opembedza 
mafano (kuvomera) Zimene 
ukuwaitanira. Mulungu 
Amadzisankhira amene wam'funa 
ndipo Amamuongolera amene 
Akutembenukira kwa lye. 

14. Ndipo sadagawikane (pa 
chipembedzo Otsatira a aneneri 






<S2 









^&&$&!$&y* \*j 



Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1043 



tdt>l it iSjj±S\ o jr - 



oyamba) kufikira Pamene 
kudawadzera kudziwa kwa 
Choonadi, chifukwa chachidani 
ndi Dumbo pakati pawo. 
Kukadapanda Liwu lochokera kwa 
Mbuye wako pachiyambi 
(Lowachedwetsera chilango) 
mpaka Nthawi yoikidwa 
kukadaweruzidwa pakati Pawo 
koma ndithu, amene adalandira 
Buku Pambuyo pawo (makolo 
awo, Ndipo ndikukumana ndi 
nthawi yako,) Ali mchikaiko 
cholikaikira (buku lawo). 

15. (Chifukwa cha umodzi wa 
zipembedzo Ndikuti pasakhale 
kugawikana pa Chipembedzo) 
choncho aitanire (Ku chipembedzo 
chimodzi); ndipo Lungama 
(poitanapo) monga momwe 
Walamulidwira. Ndipo usatsatire 
zofuna zawo. Ndipo nena: 
"Ndakhulupirira mmabuku onse 
Omwe adawavumbulutsa 
Mulungu; ndipo Ndalamulidwa 
kuchita chilungamo Pakati panu. 
Mulungu ndiye Mbuye Wathu 
ndiponso Mbuye wanu; ife tili Ndi 
ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa 
Nazo); inunso muli ndi ntchito 
zanu (Zomwe mudzalipidwa nazo). 
Palibe Kukangana pakati pa inu 
ndi ife (Chifukwa chakuonekera 
poyera Choona).Mulungu 
adzatisonkhanitsa (Kuti atiweruze); 
kwa lye yekha ndiko Kobwerera. 












Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1044 



Y p jir\ i Y ^]j-SJt 5j^ 



16. Ndipo amene akutsutsana 
ndi Mulungu pambuyo 
povomerezedwa (Ndi anthu 
ambiri), Mtsutso wawo 
ndiwachabe kwa Mbuye Wawo; 
mkwiyo waukulu (wa Mulungu) 
Uli pa iwo. Ndipo iwo adzakhala 
ndi Chilango chokhwima. 

17. Mulungu ndi Amene 
Wavumbulutsa Buku (la Qur'an 
ndi Mabuku ena) moona ndi 
Mwachilungamo. Nanga kodi 
nchiyani Chikudziwitse kuti 
mwina tsiku la Kiyama lili pafupi? 

18. (Limene) akulifulumizitsa 
amene Sakulikhulupirira; koma 
amene Akhulupirira ali oopa za 
tsikulo, ndipo Akudziwa kuti 
chimenecho nchoonadi, (Za 
kupezeka kwake palibe chikaiko). 
Dziwani kuti ndithu, amene 
akutsutsana Za nthawi (ya 
Kiyama) ali mkusokera Konka 
nako kutali. 

19. Mulungu Ngoleza kwa 
anthu Ake. Amapereka riziki kwa 
amene Wamfuna.Ndipo lye ndi 
Wamphamvu zoposa; Wopambana. 

20. Amene akufuna, pantchito 
yake, mphoto Ya tsiku lomaliza, 
timuonjezera Mphoto yakeyo; 
ndipo amene akufuna, Pantchito 
yake yabwino, mphoto ya 
Chisangalalo cha m'dziko lapansi, 












*H&b&^m'& 



hl''\\i.'-H\'l' 






Surat 42. Ash-Shiira Juzu 25 



1045 



To *jJUi 



i Y iS^^\ 0jj~- 



Timpatsa chimene chidagawidwa 
kwa iye, Ndipo iye sadzakhala ndi 
gawo (La zabwino) patsiku 
lomaliza. 

21. Kodi iwo alinayo milungu 
imene Idawakhazikitsira 
m'zipembedzo Zimene Mulungu 
sadaziloleze? Ndipo Pakadapanda 
kutsogola (lonjezo lochedwetsa) 
Liwu la chiweruzo (Mpaka patsiku 
la Kiyama); Pakadaweruzidwa 
pakati pa okanira Ndi okhulupirira 
(pompano padziko Lapansi). 
Ndipo ndithu, achinyengo Chili pa 
iwo chilango chowawa. (Cha 
Mulungu). 

22. Udzawaona (tsiku la 
Kiyama) amene Adadzichitira 
okha zoipa (Popembedza mafano) 
akuopa Chifukwa cha (zoipa) 
zomwe adachita, Ndipo 
(chilangocho) chidzawapezabe. 
Koma amene adakhulupirira ndi 
kuchita Zabwino (udzawaona 
akusangalala) Mmadimba abwino 
a ku Minda ya Mtendere. Iwo 
akapeza chilichonse chimene 
Akafune kwa Mbuye wawo. 
Umenewo Ndiwo ulemelero 
wawukulu. 

23. Umenewu ndi (ulemerero) 
umene Mulungu 
Akuwasangalatsira akapolo Ake 
nkhani Yabwino; amene 
akhulupirira ndi Kuchita zabwino. 












Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1046 



to frjJt-i 1 1 tf jyJi oj>- 



Nena (iwe Mtumiki{SAW} kwa 
iwo): "Sindikupemphani malipiro 
(kapena chuma) Pofikitsa uthenga 
(kwa inu), koma kuti Musunge 
chikondi pachibale chimene Chili 
pakati pathu. (Musandizunze 
Kufikira ndifikitse kwa inu 
uthenga wa Mbuye wanga.)" 
Amene achita Chabwino 
timuonjezera pachabwinocho 
Ndithu, Mulungu Ngokhululuka 
Kwambiri Ngolandira kuthokoza. 

24. Kapena akunena kuti: 
"Wampekera Mulungu 
Bodza?"Mulungu akadafuna 
Akadadinda mumtima mwako 
(Kuti usathe kunena chilichonse; 
koma Kuti chilichonse chimene 
ukunena Chikuchokera kwa lye). 
Ndipo Mulungu amachotsa chaboza 
(shirik), Ndi kuchilimbikitsa 
choona (Chisilamu), ndi mau Ake 
(Amene adawavumbulutsa kwa 
Mneneri Wake). Ndithu, lye 
Ngodziwa zobisika za mmitima. 

25. Ndipo lye (yekha) ndi 
amene Amavomereza kulapa 
kuchokera Kwa akapolo Ake. Ndipo 
amakhululuka Machimo (awo); 
komanso Akudziwa zimene 
mukuchita. 

26. Ndipo lye (Mulungu) 
akuwayankha Amene akhulupirira 
ndi kuchita Zabwino; ndi 
kuwaonjezera Ubwino Wake. 






$ 9 h i»t< 












Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1047 



Y o t.jlf\ I Y c£jj-SJ! 5jj~> 



Koma okanira Chilango chaukali 
chili pa iwo. 

27. Mulungu akadachulukitsa 
riziki (chuma) Kwa akapolo Ake 
onse (monga anthuwo Akufunira), 
akadapyola malire (ndi Kuononga) 
padziko; koma Mulungu Akutsitsa 
(chumacho) mwamuyeso Monga 
momwe iye afunira Ndithu, lye pa 
za akapolo Ake Ngodziwa. 
Ngopenya. 

28. Ndipo Iye yekha ndi amene 
akutsitsa Mvula atataya mtima (pa 
zamvulayo); Ndipo amafalitsa 
madalitso Ake Ndipo ndi 
Mthandizi Wotamandidwa. 

29. Ndipo zina mwa zisonyezo 
Zake ndi Kulenga kwa thambo ndi 
nthaka, ndi Zamoyo zimene 
wazifalitsa mmenemo (Zooneka 
ndi zosaoneka). Ndipo Iye ndi 
Wamphamvu zowasonkhanitsira 
(Anthu kuchokera ku imfa) 
akadzafuna. 

30. Ndipo mavuto amtundu 
Uliwonse amene akukupezani 
Nchifukwa cha (zochita zoipa) 
Zimene achita manja anu, koma 
(Mulungu) akukhululuka zambiri. 

31. Ndipo simungathe 
kum'lepheretsa (Mulungu 
kukutsitsirani mavuto) padziko 
Lapansi (ngati mutachimwa); 



®$&&\ 



J* 












%£j\£ZZ ^$£AyS&LoiS 



<a 



*.'? 9' \9%9<" 



l^Mj 






Surat 42. Ash-Shiira Juzu 25 1048 *° ^j^ 



1 1 cSjj-^l *JJ~* 



ndipo inu Mulibenso mthandizi 
kapena mpulumutsi Kupatula 
Mulungu. 

32. Ndipo zina mwa zisonyezo 
Zake ndi Zombo zoyenda panyanja 
zonga Mapiri ataliatali (koma 
osabira). 

33. Atafuna akhoza kuimitsa 
mphepo Choncho nkungokhala 
duu, (osayenda) Pamwamba pake 
(nyanja). Ndithu, mzimenezi muli 
Zisonyezo kwa aliyense Wopirira 
ndi wothokoza. 

34. Kapena akhoza kuziononga 
(potumiza mphepo Yamkutho) 
chifukwa cha machimo amene 
Adawachita. Koma amakhululuka 
zambiri. 

35. Ndipo adzadziwa (tsiku la 
Kiyama) amene Akutsutsana ndi 
zisonyezo Zathu kuti alibe 
Pothawira (kuchilango cha 
Mulungu). 

36. Ndipo chilichonse chimene 
mwapatsidwa, Nzosangalatsa za 
moyo wa padziko. Koma zimene 
zili kwa Mulungu ndi Zabwino 
ndiponso zamuyaya za amene 
Akhulupirira ndi kutsamira Kwa 
Mbuye wawo. 

37. Ndipo amene akupewa 
machimo Akuluakulu omwe 
Mulungu waletsa Ndi machimo 



¥MB'^\^^ 






&£^%£$&$#S 



©, 



\j&&<y} 






!**•!, 



*$&J&& 






Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 I 1049 I td^i it tfjysJi ojj-* 



onse oipitsitsa;ndipo iwo 
Akakwiya (chifukwa choputidwa) 
iwo Amakhululuka; 

38. Ndipo amene adayankha 
kuitana kwa Mbuye wao ndi 
kusunga mapemphero 
(Popemphera mnthawi yake 
Mkapempheredwe koyenera); 
ndipo Zinthu zawo zonse 
zimakhala zochitira Upo pakati 
pa wo; ndipo mzimene Tawapatsa 
amapereka (panjira ya Mulungu); 

39. Ndi amene Amati 
akaputidwa Amadzipulumutsa. 

40. Malipiro a choipa ndi 
choipa chonga Icho; (wochita 
choipa alipidwe Choipa chonga 
chimene wachita). Koma amene 
wakhululukira wochita Choipa 
(pomwe akhoza kubwezera), Ndi 
kuyanjana naye (mdani wakeyo), 
Malipiro ake ali kwa Mulungu; 
Ndithu, Mulungu sakonda ochitira 
Anzawo mtopola. 

41. Koma amene abwezera 
ataputidwa, Kwa iwo palibe njira 
Yowadzudzulira. 

42. Ndithu, njira 
yodzudzulidwira ili kwa Amene 
akuputa anthu ndi kudzikweza Ndi 
kuononga padziko popanda 
Chifukwa choyenera. Iwowo ndi 
amene adzalandira Chilango 
chowawa. 















Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 I 1050 I * * * >' i Y ^s)^ «j>- 



43. Ndipo amene akupirira ndi 
Kukhululuka, (Mulungu 
adzamlipira Mphoto yaikulu); 
ndithu, kupirirako Ndi chimodzi 
mwazinthu zazikulu (Chofunika 
kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa 
chikhalidwe chake.) 

44. Ndipo amene Mulungu 
wamsiya kuti Asokere, alibe 
mthandizi (wina) Kupatula lye 
Mulungu. ndipo Udzawaona 
osalungama pamene Adzachiona 
(masomphenya) chilango, 
Adzanena (modandaula): "Kodi 
pali Njira yobwerera (padziko 
lapansi kuti Tikachite zabwino 
tidzalowe ku Janna)?" 

45. Udzawaona (osalungama) 
Akusonyezedwa ku moto ali 
okhumata Chifukwa chakunyozeka 
uku akuyang'ana (Moto) 
mkayang'anidwe kobisa 
(Kotsinzina) .Ndipo amene 
Adakhulupirira adzanena pa tsiku 
la Kiyama: "Ndithu, otaika ndi 
amene Adadzitaya okha pamodzi 
ndi maanja A wo." Dziwani kuti 
osalungama Adzakhala mchilango 
chamuyaya. 

46. Ndipo sadzakhala ndi 
athangati Owapulumutsa 
(kuchilango cha moto) Kupatula 
Mulungu. Ndipo amene Mulungu 
wamusiya kuti asokere (Chifukwa 



?' ^ f :V- 1L\'<'* "" >"{' 









%£V 



Uc- 






*tf*lo#£Sto^ 



jfrVi 



Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1051 *•*>' 



t t t£jyZj\ 0j^**i 



cha zochita zake zoipa) Sangapeze 
njira (yopezera kulungama.) 

47. Muyankheni Mbuye Wanu 
lisadadze tsiku Losapeweka 
lochokera kwa Mulungu; tsiku 
limenelo Simudzapeza pothawira, 
ndipo Simudzakhala ndi njira 
(yokanira Zimene mudzachitidwa). 

48. Ngati anyalanyaza 
(Mulungu awalanga) Sitidakutume 
kwa iwo kukhala 
Muyang'aniri.Udindo wako 
Ndikufalitsa uthenga. Ndipo 
Ndithu, tikamlawitsa munthu 
mtendere Wochokera kwa Ife, 
akuunyadira (Modzikweza), koma 
choipa Chikawapeza kupyolera 
mzoipa Zimene manja awo 
adatsogoza, pompo Munthuyo 
akhala wokanira (Mulungu). 

49. Ufumu wakumwamba 
ndi padziko Lapansi Ngwa 
Mulungu; amalenga Zimene 
wafuna; amene wam'funa 
Amampatsa ana achikazi ndiponso 
Amene wamfuna amampatsa ana 
Achimuna. 

50. Kapena kuphatikiza (ana) 
achimuna Ndi achikazi (kupereka 
kwa munthu Mmodzi), ndipo 
amene wam'funa Amamchita 
kukhala chumba. Ndithu, lye 
Ngodziwa; Wokhoza 
(chilichonse). 















Surat 42. Ash-Shura Juzu 25 



1052 



ro^i tv is)^ 5j>- 



51. Nkosayenera kwa munthu 
kuti Mulungu alankhule naye 
koma Kupyolera 
mkumzindikiritsa, kapena 
Kuchokera kuseri kwa 
chotsekereza, Kapena pomtuma 
mtumiki (Jiburil) Kuti 
amvumbulutsire zimene lye 
Akufuna mwa chilolezo Chake. 
Ndithu, lye Ngwapamwamba; 
Ngwanzeru Zakuya. 

52. Momwemonso 
takuvumbulutsira Chivumbulutso 
(Chathu) mwa lamulo Lathu. 
Sudali kudziwa kuti Buku ndi 
Chiyani, chikhulupiriro ndi 
chiyani; Koma Bukuli (Qur'an) 
talichita kukhala Kuunika; ndi 
kuunikaku tikumuongola Amene 
tam'funa mwa akapolo Athu. 
Ndithu iwe ukuongolera kunjira 
Yoongoka, 

53. Njira ya Mulungu Amene 
zonse Zakumwamba ndi zamdziko 
lapansi Ndi Zake. Dziwani kuti 
zinthu zonse Zimabwerera kwa 
Mulungu. 













Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1053 



Yo*jjui trJy-ji^j^- 




SURAT AZ-ZUKHRUF XLIII 

— — -- - - ^^^HG^ L 




Surayi yayamba ndi malembo awiri; ndipo yatsatiza 
pazimenezi kufotokoza za ulemerero wa Qur'an kwa Mulungu. 
Kenako yayamba kufotokoza zamakhalidwe a achibwana 
osalabadira uthenga wa Atumiki awo. Ndipo yafotokoza 
zisonyezo zambiri zochititsa kukhulupirira mwa Mulungu 
Mmodzi. Koma ngakhale zili choncho, okanira, adampangira 
Mulungu milungu inzake ndikumpatulira lye ana aakazi, iwo 
nkudzipatulira ana aamuna. Ndipo umboni utawasowa pa 
zonena zawozi, iwo adangotsatira chikhalidwe cha makolo awo. 

Kenako Surayi yafotokoza nkhani ya Ibrahima ndikutsatiza 
pankhaniyo kudzitukumula kwa okanira a m'Makka chifukwa 
chomvumbulukira Qur'an Muhammad (SAW) osati mmodzi wa 
olemekezeka a mmizinda yawo iwiri (Makka ndi Twaif), ngati 
kuti iwo ndi amene amagawa zaufulu wa Mulungu. Mulungu 
adagawa pakati pawo riziki (chuma) chifukwa cha kusatha 
kwawo kugawa. Nanga za uneneri wa Mulungu angamgawire 
chotani amene sanamfune? 

Kenako Surayi yanenetsa kuti kukadapanda kuopera kuti anthu 
angamkanire Chauta onse, akadawapatsa okanira zosangalatsa 
zonse pamodzi ndi zokongoletsa zamdziko; okhulupirira 
nkudzawapatsa chisangalalo cha muyaya chatsiku lomaliza. 
Ndiponso yafotokoza kuti amene salabadira choonadi, Mulungu 
amamtumizira Satana yemwe amamtsogolera kuchionongeko. 

Kenako Surayi yafotokoza zankhani ya Musa ndi Farawo, ndi 
kunyengedwa kwa Farawo chifukwa cha ufumu wake. Ndi 
chilango cha Mulungu chimene chidamtsikira Farawoyo. Ndipo 
yapitirira ndi kunena nkhani ya mwana wa Mariamu kuti iye ndi 
munthu wodalitsidwa ndi Mulungu; adali kuitanira ku njira 
yolunjika ndikuopseza za chilango cha tsiku la Kiyama, ndi 
kuwauza nkhani yabwino okhulupirira ponena kuti akalowa ku 
Munda wa Mtendere, mmene muli zonse zokondweretsa. 

Pomaliza Surayi ikunena za ufumu wa Mulungu kuti zonse 
nza Iye yekha. Ndikuti milungu imene amamphatikiza nayo 
njopanda mphamvu, yachabechabe. 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 1054 t o ^jJUi 



tV u3yJ-jjl ajj*j 



Surat Az-Zukhruf XLII1 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim. 

2. Ndikulumbirira Buku 
Lofotokoza momveka. 

3. Ndithujfe talichita Bukuli 
(Qur'an) kukhala Chowerengedwa 
m'Chiarabu kuti Muzindikire. 

4. Ndipo ndithu, Bukuli 
(Qur'an) lachokera M'maziko a 
mabuku onse (Lawhi Mahfudh) 
amene adachokera kwa Ife; ndipo 
ndi Buku lotukuka, La mawu 
anzeru 

5. Kodi tisiye kukukumbutsani 
chifukwa Chakuti ndinu anthu 
opyola malire (Pochita zoipa)? 

6. Ndipo tidatumiza aneneri 
ambiri kwa Anthu akale, 

7. Ndipo palibe mneneri 
aliyense amene Amawadzera koma 
amam'chitira Chipongwe. 

8. Choncho tidawaononga 
amene Adali amphamvu kuposa 
iwo (Akuraish) Ndipo afika 
mafanizo a zilango Zomwe 
zidawapeza anthu akale. 

9. Ndipo ukawafunsa: "Ndani 
adalenga thambo ndi Nthaka?" 






Q^lfc^l^lj 









^MS^^i^^sf 












^#$&EUW3&Sft 



(^%o^(?^Irj<V3Uc^i 



Siirat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1055 to^i 



i T ^j*^ 5j>-» 



Ndithu, ayankha Kuti: "Adazilenga 
(Mulungu) Mwini Mphamvu, 
Wodziwa." 

10. Amene wakupangirani 
Nthaka kukhala monga Choyala 
ndipo adakupangirani Njira 
mmenemo kuti muongoke 
(Ndikukafika kumene mukufuna); 

11. Ndiponso Amene watsitsa 
madzi Kuchokera kumwamba 
Mwamuyeso; chifukwa cha 
Madziwo tidaukitsa mudzi 
Wakufa. Momwemonso inu 
Mudzatulutsidwa (mmanda); 

12. Ndiponso Amene walenga 
zinthu zonse Ziwiriziwiri, 
(chachimuna ndi Chachikazi). 
Ndipo adakupangirani Zombo ndi 
ziweto zimene mukukwera, 

13. Kuti mukhazikike 
mwaubwino Pamisana paizo, 
kenako mukumbukire Mtendere 
wa Mbuye wanu Mukakhazikika 
pamenepo, ndipo Munene: 
"Walemekezeka Amene 
Watifewetsera ichi; ndipo 
sitikadatha Kuchifewetsa ndi 
kuchigwiritsa ntchito. 

14. Ndipo ndithu, ife kwa 
Mbuye wathu ndiko tidzabwerera." 

15. Ndipo amuikira gawo Mwa 
akapolo Ake. (Kuti ndi ana a 
Mulungu.) Ndithu munthu, 
Ngwamsulizo woonekera poyera! 



?*\'\iK* ' 9 i\ * 9£f* 



W^e 


















Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1056 



to^t tr «J^jJiSj>- 



16. Kodi wadzichitira ana 
achikazi Mzimene wazilenga 
ndipo Wakusankhirani inu ana 
achimuna? 

17. Koma akauzidwa (kuti 
wabereka mwana Wachikazi) 
mmodzi wa iwo chomwe 
Amamfanizira (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri, nkhope 
Yake imakhala yakuda Ndi 
kudandaula kwambiri! 

18. Ha! Kodi amene watered wa 
monga Chokongoletsa, potsutsana 
iye sangathe Kunena momveka? 
(Ameneyo ndiye Mwampatsa 
Mulungu; omwe ndi ana Achikazi). 

19. Ndipo angelo omwe ndi 
akapolo a (Mulungu) Wachifundo 
chambiri Akuwatcha akazi.Kodi 
adaona kalengedwe Kawo? 
Umboni wawo ulembedwa Ndipo 
adzafunsidwa (pazimenezo)! 

20. Ndipo (okanira) akunena: 
"Akadafuna (Mulungu) 
Wachifundo chambiri (kuti 
Tisamapembedze mafano awa), 
Sitikadawapembedza!" Iwo alibe 
kudziwa pazimenezi (zomwe 
Akunenazi). Koma akungonena 
mawu Opeka. 

21. Kapena tidawapatsa Buku 
lina tisadapereke Hi, kotero kuti 
iwo akugwiritsa Limenelo (ndi 
kugwirizana nazo Zili mmenemo)? 



$&*&&&&$ 



© ( 






J^d&*S$<Xti&& 



®&#. 



f *& 






*' 









Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1057 *•*>» ir^jr}\*^ 



22. Koma akunena: "Ndithu, ife 
Tidawapeza atate athu pa 
Chipembedzo Chimenechi, ndipo 
ife Tikutsatira mapazi awo," 

23. Ndipo momwemo, 
sitidatumize mchenjezi Patsogolo 
kumudzi uliwonse koma Olemera 
ammenemo adanena: "Ndithu, 
tidawapeza atate athu Pa 
chipembedzochi (akuchita 
mmene Tikuchitiramu), ndipo ife 
titsatira Mmapazi awo." 

24. Adanena (mneneri wawo): 
"Ngakhale Ndakubweretserani 
chipembedzo Chabwino kuposa 
chomwe Mudawapeza nacho atate 
anu (Mupitirizabe kutsatira 
chipembedzo Cha makolo 
anucho)?" Adanena: "Ife tikuzikana 
zimene Mwatumidwa nazozi." 

25. Choncho tidawalanga iwo. 
Taona m'mene adalili Mapeto a 
otsutsa aja. 

26. Ndipo (kumbuka) pamene 
Ibrahim Adauza bambo wake ndi 
anthu ake (kuti): "Ndithu, ine 
ndadzipatula kuzimene 
Mkuzipembedzazi, 

27. Kupatula Amene 
Adandilenga; ndithu, lye 
andiongola." 

28. Ndipo adalichita liwu ili 
kukhala Losatha ku mtundu wake, 












© <&££M$ 32*<$$fcSl 



J&itf&gfc&fc} 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1058 



to *jjfe.| 



tv ciyj-jii 3jj-*> 



Kuti abwerere (Ku malankhulidwe 
amenewa). 

29. Koma ndidawasangalatsa 
awa (Akuraish) pamodzi ndi atate 
awo Kufikira choonadi 
chawadzera ndi Mtumiki 
wolongosola (za choonadichi). 

30. Ndipo pamene choonadi 
(Qur'an) chidawadzera, adanena: 
"Awa ndi matsenga; ndithu, ife 
Tikuakana." 

31. Ndipo adatinso: 
"Nchifukwa ninji Qur'an iyi 
siidavumbulutsidwe Pamunthu 
wamkulu Mmidzi iwiriyi (Makka 
ndi Taif,)" 

32. (Choncho Mulungu 
akunena): "Kodi Iwo ndi amene 
akugawa mtendere wa Mbuye 
wako (kumpatsa amene Wamfuna 
ndi kumana amene sakufuna 
Kumpatsa? Chikhalirecho) Ife ndi 
Amene timagawa pakati pawo 
zofunika Pamoyo wawo mu moyo 
wadziko Lapansi; ndipo 
tawatukula ena mwa iwo Pa 
ulemerero pamwamba pa ena, 
Choncho ena mwa iwo akuwachita 
Anzawo kukhala antchito awo 
Koma mtendere wa Mbuye wako 
ndi wabwino kuposa Zimene 
akusonkhanitsa. 

33. Ndipo pakadapanda kuopera 
kuti anthu Adzakhala gulu limodzi 


















fc^j.ts«&j|<asir; 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1059 I t © ,>i it Jj^ jli 5^ 



(lokanira Mulungu), ndithu, 
tikadazichita Nyumba za amene 
akumkana (Mulungu) Wachifundo 
Chambiri kukhala ndi Madenga a 
Siliva, ndi makwerero Amene 
amakwerera (Kukhalanso a Siliva), 

34. Ndipo nyumba zawo 
kukhala ndi zitseko Ndi makama 
(mabedi) amene Amayadzamira 
(zonse Kukhala za Siliva), 

35. Ndiponso ndi zokongoletsa 
za golide. Koma zonsezo sikanthu 
ayi, ndi Chisangalalo chabe chadziko 
lapansi (Chosakhalira kutha); 
ndipo tsiku Lomaliza lomwe lili 
kwa Mbuye wako Ndi la oopa 
Mulungu (potsatira Malamulo Ake 
ndi kusiya zoletsedwa). 

36. Ndipo amene akunyozera 
kukumbukira (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri, Timpatsa 
Satana, kuti iye akhale Bwenzi 
lake (lotsagana nalo). 

37. Ndipo iwo amawatsekereza 
kunjira Zabwino ndi kumaganiza 
Kuti iwo ngoongoka. 

38. Kufikira pamene 
adzatidzera (Tsiku la Kiyama, uku 
akulowetsedwa Ku moto). Adzati 
(kumuuza Satana): "Kalanga ine! 
Pakati pa iwe ndi ine Pakadakhala 
mtunda wa pakati pa Kuvuma ndi 
kuzambwe (kutalikirana Kwathu)." 
Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi! 






^m&&%$v& 






i< **t\ \9 4i. 9S 9' \j>* 9" 






Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1060 



to frjA-i tr cJy-jJidjj-- 



39. (Mulungu adzawauza kuti): 
"Ndipo lero Sikukuthandizani 
kukhala limodzi kwanu M'chilango 
pakuti mudadzichitira nokha Zoipa. 

40. Kodi ungathe kuwamveretsa 
Agonthi, kapena ungathe 
Kuwaongola akhungu ndi amene 
Ali mkusokera koonekera? 

41. Ngati titakuchotsa (padziko 
usadaone Chilango chawo, 
usakhale ndi chikaiko), Ndithu, Ife 
tiwalanga iwo, 

42. Kapena tikusonyeza zimene 
Tidawalonjeza (uona ndi maso ako 
Usadafe). Ndithu, Ife till ndi 
mphamvu Pa iwo. 

43. Choncho, gwiritsa zimene 
Zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu, 
iwe Uli panjira yolunjika. 

44. Ndithu, iyi (Qur'an) ndi 
ulemerero Wako ndi anthu ako; 
ndipo posachedwa Mufunsidwa 
(za ulemerero umenewu). 

45. Ndipo afunse aneneri Athu 
amene Tidawatumiza iwe usadadze: 
"Kodi Tidapanga milungu ina kuti 
Ipembedzedwe, osati Mulungu 
Wachifundo Chambiri?" 

46. Ndithu, tidamtumiza Musa 
pamodzi Ndi zozizwitsa Zathu 
kwa Farawo Ndi nduna zake; ndipo 
adati: "Ndithu, ine ndine Mtumiki 
wa Mbuye wa zolengedwa." 






&&&$$ify®®sii 



$*%&&&&%& 

®"'>& 












Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 1061 I * o ^i i r *Jj*^ 5j>- 



47. Koma pamene adawadzera 
Ndi zisonyezo zathu, basi Iwo 
adali kuziseka. 

48. Ndipo chisonyezo 
chilichonse chomwe 
Tidawasonyeza chidali chachikulu 
Kuposa chinzake (komabe 
Sadakhulupirire). Ndipo 
tidawalanga Ndi chilango kuti 
abwerere (kwa Ife). 

49. Ndipo adati (kwa Musa): 
"E, iwe Wamatsenga! Tipemphere 
Kwa Mbuye wako pachomwe 
Adakulonjeza; ndithu, ife 
Tiongoka, (tikhulupirira)." 

50. Choncho, pamene 
tidawachotsera Chilangocho, basi 
iwo adayamba Kuswa pangano. 

51. Ndipo Farawo adaitana 
anthu ake, Adati: "E, inu anthu 
anga! Kodi Ulamuliro wa mu 
Iguputo Siwanga pamodzi ndi 
mitsinje iyi Imene ikuyenda pansi 
panga (pa nyumba Zanga?) Kodi 
simukuona? 

52. Kodi kapena ine sindine 
woposa uyu (Musa) wonyozeka, 
Ndipo sangathe Kulankhula 
momveka? 

53. Nanga bwanji sadapatsidwe 
Zibangiri zagolide kapena Angelo 
kudza pamodzi Ndi iye uku 
akumtsatira?" 















t&£ %j$\^&j&*1 









Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1062 I to,>i 



it Jy-jJl «jj~» 



54. Adawapeputsa anthu ake. 
Ndipo Adamvera; iwo adali anthu 
otuluka Mchilamulo (cha Mulungu). 

55. Pamene adatikwiitsa, 
tidawalanga Ndipo tidawamiza 
mmadzi onse. 

56. Tidawachita (Farawo ndi 
anthu ake) Kukhala chitsanzo cha 
okanira A pambuyo pawo 
ndikukhala mbiri Kwa anthu 
amene akudza. 

57. Ndipo pamene 
lidaperekedwa fanizo la Mwana 
wa Mariam, pamenepo anthu anu 
Adali kufuula (monyoza). 1 

58. Ndipo adati: "Kodi milungu 
yathu Ndi yabwino, kapena iye?" 
Sadamfanizire kwa iwe koma 
kufuna Kutsutsana basi (kopanda 
kufuna Choona). Koma iwo ndi 
anthu amtsutso. 

59. Iye sadali kanthu koma ndi 
kapolo Amene tidampatsa 
Mtendere; Ndipo tidamchita 
kukhala chitsanzo (Chodabwitsa) 
cha ana a Israeli. 






% 9 2$!&&3?&*jfc& 



&%&&$%&$$& 

%^^'S^i 






Fanizo lomwe likunenedwa apa ndi lomufanizira Yesu ndi zomwe 
zikupembedzedwa kusiya Mulungu. Akafiri adamfanizira iye pambuyo 
povumbulutsidwa aya yakuti: "Ndithu inu ndi zomwe mukuzipembedza kusiya 
Mulungu ndi nkhuni za ku Jahannama." Choncho adati Yesu nayenso akalowa 
ku moto chifukwa chakuti Akhrisitu amamupembedza kusiya Mulungu. Koma 
Mulungu adamyeretsa ponena kuti: "Ndithu awo amene ubwino wochokera 
kwa Ife watsogola kwa iwo, iwowo akatalikitsidwa ndi iwo (motowo)" Choncho 
Yesu sakalowa kumoto chifukwa iye sadalamule anthu kuti amupembedze 
komanso sakudziwa kuti pali aliyense amene akupembedza iye. 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1063 f**j*-» 



tT <J)jS>-^\ 5jj»*» 



60. Ndipo tikadafuna 
tikadawachita angelo Kukhala 
padziko mmalo mwa inu ndi 
Kumasiirana iwo kwa iwo (kuti 
mudziwe Kuti angelo akugonjera 
malamulo a Mulungu, iwo 
simulungu). 

61. Ndipo iye (Isa) adzakhala 
chizindikiro Cha Kiyama (kuti 
yayandikira). Choncho 
Musaikaikire, koma nditsatireni. 
Imeneyi ndi njira yolunjika. 

62. Asakutsekerezeni satana; 
iye Kwa inu ndi Mdani woonekera. 

63. Ndipo pamene Isa adadza 
ndi zisonyezo Zoonekera poyera, 
adati: "Ndakudzerani Ndi nzeru 
(yopindulitsa), ndikuti 
Ndikulongosolereni zina zimene 
Mudali kusiyana mu izo; choncho, 
Muopeni Mulungu ndiponso 
ndimvereni. 

64. Ndithu, Mulungu ndiye 
Mbuye wanga Ndi Mbuye 
wanunso; choncho 
Mupembedzeni; imeneyi ndiyo 
njira Yolunjika." 

65. Koma adapatukana pakati 
pawo Mmagulumagulu. 
Kuonongeka ndi Chilango chatsiku 
lowawa kudzakhala Kwa amene 
adzichitira okha zoipa. 

66. Palibe chimene 
akuyembekeza, koma Kiyama basi 






^ <9* 9A9* 









®. 



m&^^'*& 



x&3%&\%&3&;& 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1064 



yotj)r\ tr J/jliSj^- 



yomwe iwadzera Mwadzidzidzi 
pomwe iwo sakuzindikira (Ali 
otanganidwa ndi zam'dziko). 

67. Abwenzi tsiku limenelo 
adzakhala Odana, wina ndi 
mnzake, (chifukwa Chakuti adali 
kuthandizana pa Zinthu 
zosalungama ndi zamachimo) 
Kupatula oopa Mulungu (amene 
adachita Chibwenzi mwa 
Mulungu, pothandizana 
Kukwaniritsa malamulo a 
Mulungu ndi Kusiya zimene 
Mulungu waletsa). 

68. (Mulungu adzati): E, inu 
akapolo Anga (Abwino)! Palibe 
kuopa kwa inu lero lino Ndiponso 
simudandaula. 

69. Amene adakhulupirira 
zisonyezo Zathu Ndipo adali 
Asilamu (ogonjera Mulungu); 

70. Lowani ku Munda Wa 
mtendere, inu ndi Akazi anu 
musangalatsidwa. 

71. Adzakhala akupititsidwa 
mbale Zagolide ndi matambula 
(agolide); Zonse zokomera moyo 
zidzakhala Mmenemo ndi 
zokomera maso, ndipo Inu 
mudzakhala mmenemo muyaya. 

72. Ndipo uwu ndi munda 
umene mwapatsidwa Chifukwa 
cha (zabwino) zimene Munkachita. 



*®sa®j&3k 






$&%&$$&}$$+ 









Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1065 



Yo^jjui ir<Jj*j\*^ 



73. Inu mupeza mmenemo 
zipatso Zambiri zomwe Muzidya. 

74. Ndithu, ochimwa (okanira) 
adzakhala Mchilango cha 
Jahannama muyaya; 

75. Sadzapatsidwa nthawi 
yopumula, Ndipo mmenemo iwo 
akataya mtima (Zakupeza umoyo 
wabwino). 

76. Ndipo sitidawapondereze 
koma Adali kudzipondereza okha. 

77. Ndipo (okanira) adzaitana 
Ee, iwe Maliki (yemwe ndi 
Mngelo Woyang'anira moto): 
"Mbuye wako atipatse imfa (kuti 
Tipumule kuchilangochi!)" 
Adzanena (Malik): "Ndithu, inu 
Mukhala momwemo!" 

78. Ndithu, tidakubweretserani 
Choona; koma ambiri a inu Mudali 
kuchida choona. 

79. Kodi akonza bwino 
chikonzero (Chawocho chomwe 
ndi chiwembu Chofuna kumupha 
Mtumiki{SAW})? Ndithu, nafenso 
ndife okonza chikonzero Chabwino 
(cholepheretsa chiwembu 
Chawocho). 

80. Kodi akuganiza kuti 
sitikumva zobisa Zawo ndi 
zonong'oneza zawo? Iyayi, 
(tikuzimva zonse), ndipo Atumiki 


















Siirat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1066 



ro ^j*-i 



tY ^y-ji' ojj~> 



Athu (angelo) ali nawo Pamodzi; 
akulemba. 

81. Nena (kwa omphatikiza 
Mulungu ndi Mafano): 
"Zikadakhala kuti (Mulungu) 
Wachifundo Chambiri ali ndi 
mwana, Ndiye kuti ine 
ndikadakhala woyamba 
Kumpembedza (mwanayo 
chifukwa Chakuti ndi mwana wa 
Mulungu)." 

82. Mbuye wa kumwamba ndi 
pansi,Mbuye wa Mpando 
Wachifumu, Wapatukana ndi mbiri 
zimene Akum'nenerazo (zoti 
Mulungu ali ndi Mwana). 

83. Asiye azingonena 
zachabezo ndi Kusewera kufikira 
adzakumana Ndi tsiku lawo limene 
Akulonjezedwa. 

84. Ndipo lye amene 
akupembedzedwa Kumwamba, 
ndiponso ndi lye Amene 
akupembedzedwa pansi. lye Ndi 
Wanzeru zakuya, Wodziwa 
Kwambiri. 

85. Ndipo watukuka kwambiri 
Yemwe Ufumu wa kumwamba ndi 
pansi ndi Pakati pazimenezi ndi 
Wake. Ndiponso Kwa lye ndiko 
kuli kudziwa kudza Kwa tsiku la 
Kiyama; ndipo kwa lye Yekha ndi 
kumene m'dzabwezedwa. 






J$\&L0X?1&\£6&> 


















Ha*"** 



Surat 43. Az-Zukhruf Juzu 25 



1067 



tO*j*-» tT vJytjJiSjj-- 



86, Ndipo omwe 
akuwapembedzawo kusiya lye 
(Mulungu), sangathe kupulumutsa 
(Aliyense) kupatula amene 
akuikira Umboni choonachi, 
pom we iwo Akuchidziwa bwino. 

87, Ndipo ngati utawafunsa: 
"Ndani Adawalenga?" Anena 
motsimikiza kuti: "Ndi Mulungu". 
Nanga akutembenuzidwa Bwanji 
(kusiya choona)? 

88. Ndipo zonena zake 
(Mneneri Muhammad {SAW} 
nthawi zonse) "E, Mbuye Wanga! 
Ndithu, awa ndi anthu 
Osakhulupirira". 

89. Choncho, akhululukire, 
ndipo auze Mawu a mtendere. 
Posachedwa Adzadziwa! 






&l<? 






i#S<& 










Surat 44. Ad-Dukhan Juzu25 



1068 



to *j*-l 



i i ObJ-oil 0jj-» 




Surayi yayamba ndi kufotokoza za Qur'an kuti 
idavumbulutsidwa kuchokera kwa Mulungu, mu usiku wa 
Lailatul Qadir, usiku wodala, ndi cholinga chochenjeza ndi 
kulongosola umodzi wa Mulungu. 

Ndithu, Qur'an ndi choona chochokera kwa Mulungu. Ndipo 
Surayi yafotokozanso za kuuka ponenetsa kuti palibe chikaiko 
kuukako kulipo. Ndipo okanira yawadzudzula pamitsutso yawo 
yopanda pake ndi kufanizira okanira a mMakka ndi anthu akale, 
anthu a Farawo. Ndipo yatsimikiza ndi kulonjeza kuti tsiku la 
Kiyama ndilo tsiku lawo lolonjezedwa kuweruzidwa kwawo 
onse. Ndipo yafotokoza zamphoto ya osokera, ndi mphoto ya 
olungama pa tsiku limeneli. 

Surayi yamaliza ndi kufotokoza za Qur'an monga idayambira 
kufotokoza za Qur'aniyo. 




Surat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 I 1069 I t e *j*-» £ i Oi^jJi Sjj- 



Surat Ad-Dukhan XLIV 



; qj^^T**- 






^^ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim. 

2. Ndikulumbirira Buku 
lofotokoza Momveka. 

3. Ndithu, tidaivumbulutsa 
(Qur'an) mu Usiku wodala. Ife 
ndithu Ndiachenjezi. 

4. Mu (usiku) umenewu chinthu 
Chilichonse chanzeru 
chimaweruzidwa Ndi 
kulongosoledwa 

5. Mwa Chilamulo chochokera 
kwa Ife. Ndithu, Ife Ndife otumiza 
Atumiki (Kuti achenjeze anthu). 

6. (Chifukwa cha) chifundo 
chochokera Kwa Mbuye wako. 
Ndithu lye Ngwakumva zonse, 
Wodziwa kwabasi; 

7. Mbuye wa thambo ndi nthaka 
ndi Zapakati pake, ngati Muli 
otsimikiza. 

8. Palibe wopembedzedwa moona 
koma lye basi.Amapereka moyo 
ndikupereka Imfa, Mbuye wanu 
ndi Mbuye wa makolo anu oyamba. 

9. Koma iwo (okanira) ali 
mchikaiko Akungosewera, 
(potsatira Zilakolako zawo zoipa). 



o^lc^jll^U. 



& 



A > r- 






*^««fe£*2Ga 



^%&$tyty%tf% 






Surat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 1070 * ° *j^ s * * ai^aJi 5 j>* 



10. Basi, yembekezera tsiku 
limene Thambo lidzadze Ndi utsi 
woonekera (Konsekonse), 

11. Udzawaphimba anthu onse 
(ndipo Adzakhala akunena:) "Ichi 
ndi chilango Chowawa. 

12. E, Ambuye! Tichotsereni 
Chilangochi, ndithu, Ife 
tikhulupirira." 

13. (Kodi lero) kukumbukira 
kuwapindulira Chiyani iwo, 
chikhalirecho mtumiki Wolongosola 
chilichonse adawadzera. 

14. Koma sadamlabadire uku 
akumnena Kuti: "Waphunzitsidwa 
(ndi anthu), Ndiponso wopenga." 

15. Ndithu ife tichotsa 
chilangocho pang'ono (Koma) inu 
mubwerezanso (Machimo anu). 

16. (Kumbuka, iwe Mtumiki), 
tsiku limene Tidzawalanga 
chilango chachikulu; Ndithu, Ife 
ndife olanga. 

17. Ndipo ndithu, iwo asadadze, 
tidawayesa Anthu a Farawo. 
Ndiponso adawadzera Mtumiki 
wolemekezeka, 

18. Kuti: "Ndipatseni akapolo a 
Mulungu. Ndithu, ine kwa inu ndi 
Mtumiki Wokhulupirika; 

19. Ndipo musadzikweze kwa 
Mulungu. Ndithu, ine 



^^fc»$3#K 



<#6&& k <j^lJ&< 



^j^a8t\&a^ 






&&&&$&&$& 



® 












Siirat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 1071 t o t£\ it d\*jS\ 5j^ 



ndikubweretserani Chisonyezo 
choonekera. 

20. Ndipo Ine ndadzitchinjiriza 
ndi Mbuye Wanga ndiponso 
Mbuye wanu (Ku chiwembu 
chofuna kundipha) Pondigenda 
(ndi miyala). 

21. Ndipo ngati 
simundikhulupirira, Ndipatukeni 
(Musandi vutitse) . " 

22. (Koma adamchitira 
mtopola). Ndipo lye adaitana 
Mbuye wake kuti: "Awa ndi anthu 
oipa." 

23. (Mulungu adamuuza kuti): 
"Pita ndi akapolo Anga usiku; 
ndithu, inu Mulondoledwa. 

24. Ndipo isiye nyanja ili 
momwemo, zii. Ndithu, iwo ndi 
khamu (lankhondo) Limene 
limizidwa." 

25. Kodi ndi minda ingati ndi 
akasupe Zomwe adazisiya 
atamizidwa, 

26. Ndiponso mmera ndi malo 
abwino. 

27. Ndi mtendere (waukulu) 
umene adali Kusangalala nawo 
mmenemo. 

28. Umo ndi mmene zidalili. 
Ndipo tidawapatsa anthu ena 
zimenezo. 









Surat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 



1072 



Y o fr jJUi t i Ob^aJi 5jj-- 



29. Thambo ndi nthaka 
sizidawalirire Ndipo sadapatsidwe 
mpata (Wobwereranso padziko). 

30. Ndipo ndithu, tidapulumutsa 
ana a Israeli ku chilango Choyalutsa, 

31. Chochokera kwa Farawo; 
ndithu, iye Adali wodzikweza 
ndiponso mmodzi Wa opyola 
malire. 

32. Ndipo ndithu, tidawasankha 
(Ayuda Nthawi imeneyo) pamitundu 
ina M'kudziwa Kwathu, 

33. Ndipo tidawapatsa 
zisonyezo (Kupyolera m'dzanja la 
Musa) momwe Mudali mayeso 
oonekera poyera kwa I wo. 

34. Ndithu, awa (Akuraish) 
akunena(kuti): 

35. "Palibe china choposera pa 
imfa yathu Yoyambayi, ndipo Ife 
sitidzaukitsidwa. 

36. Choncho tibweretsereni 
makolo athu (Amene adafa), ngati 
mukunena Zoona (kuti kuli kuuka)." 

37. Kodi iwo ndi abwino (ndi 
kupambana Panyonga), kapena 
anthu a Tubba (Mafumu a kudziko 
la Yemen) ndi Amene adalipo kale 
iwo asadadze? Tidawaononga. 
Ndithu, iwo adali oipa. 

38. Ndipo sitidalenge thambo 
ndi nthaka Ndi zimene zili pakati 
paizo, Mwachibwana. 









^<frW-#»$ 



^ifow^&^j 



fess$*a 












Siirat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 1073 Y o ^jA-t 



i i Ol^-oJl Sjj-*. 



39. Sitidalenge ziwirizi Koma 
mwachoonadi; Koma anthu ambiri 
sakudziwa. 

40. Ndithu, tsiku lachiweruzo 
Ndiyo nthawi yawo onse (Imene 
alonjezedwa), 

41. Tsiku limene m'bale 
sadzathandiza M'bale wake pa 
chilichonse (ku Chilango cha 
Mulungu), Ngakhale iwo 
sadzapulumutsidwa. 

42. Kupatula amene Mulungu 
Adzawachitira chifiindo. Ndithu, lye 
Ngwamphamvu zoposa, Wachisoni. 

43. Ndithu, mtengo wa Zakkumi, 

44. Ndi chakudya cha ochimwa; 

45. (Kutentha kwake) ngati 
mtovu Wosungunulidwa, 
(wotentha Kwambiri;) 
udzakhala ukuwira Mmimba, 

46. Monga kuwira kwa madzi 
otentha Kwambiri. 

47. (Kudzanenedwa): 
"Mgwireni; Mkokereni (ndi 
kumponya) Pakatikati pa Jahena! 

48. Kenako mthireni 
pamwamba pamutu Wake chilango 
chamadzi otentha! 

49. (Adzauzidwa 
mwachipongwe): "Lawa! Ndithu, 
iwe ndiwe wamphamvu Zambiri, 















Surat 44. Ad-Dukhan Juzu 25 I 1074 t o *>» it Obs-oli Sjj~- 



wolemekezeka, (monga Momwe 
udali kudzitamira muja). 

50. Ndithu, izi ndi zimene 
mudali Kuzikaikira zija!" 

51. Ndithu oopa Mulungu 
adzakhala Pamalo a chitetezo, 

52. Mminda ndi mu akasupe; 

53. Adzavala (nsalu) za silika 
Wopyapyala ndi silika Wokhuthala 
uku atayang'anizana (Nkhope); 

54. Umo ndi mmene zidzakhalire; 
ndipo Tidzawakwatitsa ndi 
Ahuri'aini (Akazi okongola amaso 
aakulu). 

55. Mmenemo adzakhala 
akuitanitsa Mtundu uliwonse wa 
zipatso, Mwamtendere; 

56. Mmenemo sadzalawa imfa, 
kupatula Imfa yoyamba ija; ndipo 
Adzawateteza Kuchilango cha 
Jahena, 

57. Chifukwa cha chifundo 
chochokera Kwa Mbuye wako! 
Kumeneko ndiko Kupambana 
kwakukulu! 

58. Ndithu, taifewetsa (Qur'an) 
Mchiyankhulo chako (cha 
Chiarabu) Kuti akumbukire. 

59. Choncho yembekeza; iwonso 
Akuyembekezera, (kodi ndani 
Chimtsikire chilango pakati panu!). 






<*? 9>l& A'*i 






<oy&^*&v*w* 



Surat 45. Al-Jathiyah Juzu25 1075 I to *>! 



I o aJ\±-\ 5jj-*> 



T^T' 



* 



•knfc&vF^'tti 



SURAT AL-JATHIYAH XLV_ 

j^b- - , — - " .— -z^J^-^* 1 ^ ^ET^^Ei 



Surayi ikufotokoza zamafuwa a chikhulupiriro cha Chisilamu, 
mmbali zake zonse zophanuka:- Kukhulupirira Umodzi wa 
Mulungu; kukhulupirira Qur'an ndi utumiki wa Mtumiki 
Muhammad (SAW); kukhulupirira za tsiku lomaliza ndi kuuka 
ku imfa ndi kuweruzidwa pa zochita. 

Nkhani yaikulu msurayi ndi kupereka umboni ndi zisonyezo 
zosonyeza Umodzi wa Mulungu. 

Ndipo Surayi yayamba ndi kunena za Qur'an ndi gwero lake 
lomwe ndi kwa Mulungu Wamphamvu zoposa; Wanzeru zakuya pa 
zolenga Zake; Yemwe adavumbulutsa Buku Lake lolemekezeka 
kuti likhale mtendere kwa anthu Ake ndikuti likhale muuni 
wounikira anthu ku njira ya mtendere. 

Kenako yafotokoza za zisonyezo za chilengedwe zomwe 
zikusonyeza mphamvu ya Chauta ndikuti alipo; zomwenso 
zikupezeka ponseponse mdziko ili lophanuka. 

Ndipo yanenanso zakalengedwe ka anthu ndi nyama ndi 
zolengedwa zina zosiyanasiyana zomwe zikusonya Mulungu; 
monga: kusinthana usiku ndi usana, kukuntha kwa mphepo 
motembenukatembenuka; ndipo zonsezi zikusonyeza mphamvu 
ndi ulemelero waukulu wa Mulungu. 




Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 I 1076 I * ° *j*-* 



i o Uli-i 5jj-* 



Surat Al-Jathiyah XLV 



y— ■■-■ ■■-■■ 



, ^^ 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim. 

2. Chivumbulutso cha Buku (ili) 
Chochokera kwa Mulungu 
Wamphamvu zoposa, Wanzeru 
zakuya. 

3. Ndithu, kuthambo ndi 
m'nthaka muli Zisonyezo 
(zazikulu zosonyeza kuti Mulungu 
alipo) kwa okhulupirira. 

4. Ndiponso mkalengedwe kanu 
ndi Kalengedwe kazimene 
wazifalitsa Mmenemo, (monga 
zamoyo ndi Zopanda moyo), muli 
zisonyezo Kwa anthu amene 
akutsimikiza. 

5. Ndi kusinthana kwa usana 
ndi usiku, Ndi mvula imene 
Mulungu Akutsitsa kuchokera 
kumwamba, Akuukitsa nthaka ndi 
mvulayo, itafa (Itauma), ndi 
kuyendetsa mphepo 
Mosinthasintha; (zonsezi) ndi 
zisonyezo Kwa anthu anzeru. 

6. Izi ndi aya (ndime) za 
Mulungu; Tikukuwerengera iwe 
mwachoonadi. Kodi ndi nkhani 
yanji adzaikhulupirire Atapanda 
kulabadira nkhani ya Mulunguyi 
ndi aya Zake? 



c&£\<£&\&\j>- 



i -uft 



G£i 



®Wt^s$<^ 



^k^sj&s^m 






J£5^g3^£3!^&! 

»£T9»i Ju.li .* »& ' \'*.»" *' 






Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 



1077 



to *>i 



£ o ajUt-l 5jj-*» 



7. Kuonongeka kuli paaliyense 
wopeka Zinthu, wamachimo 
ambiri; 

8. Amene akumva aya za 
Mulungu Zikuwerengedwa kwa 
iye kenako Nkumapitiriza 
(chipembedzo chake 
Chosalungama) uku akudzikweza 
ngati Kuti sadazimve ayazo; 
muuze nkhani Ya chilango 
chowawa. 

9. Ndipo akadziwa chinthu 
chochepa Chochokera mma aya 
athu, Amachichitira chipongwe; 
amenewa ndi Amene adzakhala 
ndi chilango Chosambula. 

10. Jahannama ili 
(kuwayembekezera) kuseri 
Kwawo; ndipo zimene adachita 
Sizidzawathandiza chilichonse, 
Ngakhale atetezi amene 
adadzipangira; Kusiya 
Mulungu,(sadza wathandiza) ; 
Ndipo adzapeza chilango 
chachikulu. 

11. Ichi ndi chiongoko; ndipo 
amene Adakanira aya za Mbuye 
wawo, Adzakhala ndi chilango 
chachikulu Chochokera mchilango 
chowawa. 

12. Mulungu ndi Amene 
wakugonjetserani Nyanja kuti 
zombo ziziyenda mmenemo Mwa 
lamulo Lake; ndikuti munke 



3jMfcjK& 


















Siirat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 



1078 



T© *j*-i 



t © aJUrl oj^ 



Mufunafuna chifundo Chake kuti 
Muthokoze. 

13. Ndipo wakugonjetserani za 
kumwamba Ndi zam'nthaka zonse 
zikuchokera kwa lye. Ndithu, 
mzimenezo muli Zisonyezo kwa 
anthu amene Amalingalira. 

14. Nena kwa amene 
akhulupirira kuti Awakhululukire 
amene sakuopa Masiku a Mulungu 
(a chilango; Mmasiku amenewo) 
kuti awalipire anthu Pa zomwe 
amachita (zoipa). 

15. Amene akuchita chabwino 
Akudzichitira yekha ndipo amene 
Akuchita zoipa, zidzakhala paiye 
Mwini. Kenako Mdzabwezedwa 
kwa Mbuye wanu. 

16. Ndithu, tidawapatsa Ana a 
Israeli Buku, ulamuliro ndi 
uneneri; Ndiponso tidawapatsa 
zinthu zabwino Ndikuwasankha 
pamwamba pa Mitundu ina. 

17. Ndipo tidawapatsa 
zisonyezo Zoonekera pazinthu 
zachipembedzo Chawo; 
sadapatukane mpaka pomwe 
Kudawadzera kudziwa, chifukwa 
Chadumbo pakati pawo. Ndithu, 
Mbuye wako adzalamula pakati 
pawo Tsiku la Kiyama pa zimene 
Adali kutsutsana. 

18. Kenako tidakuika iwe pa 
malamulo a zinthu za chipembedzo 



h'*Mz 









*'J&k 



t)j«^4^8ty^^tt 



w&£&&&&& 



Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 1079 to ^ 



t UUrl 5jj-*» 



(Chathu). Choncho tsatira malamulo 
(Athu oona) Usatsate zilakolako za 
amene sadziwa (Njira yoona). 

19. Ndithu, iwo (amene 
akutsata njira Zonama) 
sangakuthandize chilichonse Kwa 
Mulungu; ndithu, achinyengo Ena 
a iwo amatetezana wina ndi 
Mnzake; koma Mulungu ndi 
Mtetezi Wa oopa (lye potsatira 
malamulo Ake Ndi kusiya 
zoletsedwa). 

20. Iyi (Qur'an imene 
yavumbulutsidwa kwa iwe), 
Ndizisonyezo kwa anthu 
chiongoko ndi Chifundo kwa anthu 
omwe akutsimikiza (Kuti lilipo 
tsiku la chiweruzo). 

21. Kodi amene adadzichitira 
zoipa Akuganiza kuti tingawachite 
monga Omwe adakhulupirira ndi 
kuchita Zabwino kuti afanane pa 
moyo wawo Ndi pa imfa yawo?) 
Ndi kulamula koipa Kumene iwo 
akulamula. 

22. Ndipo Mulungu adalenga 
thambo ndi nthaka Moona ndi kuti 
mzimu uliwonse Ulipidwe zimene 
udadzichitira, (Zoipa kapena 
zabwino) ndipo iwo 
Sadzaponderezedwa. 

23. Kodi wamuona amene 
wachichita Chilakolako chake 
kukhala Mulungu Wake 



*&£&&# &s&% 















m$&ty&&&\ 



Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 1080 I t o tjJt-i 



t D UUri 3jj~* 



wompembedza? Ndipo Mulungu 
Wamlekerera kuti asokere, 
kupyolera Mkudziwa Kwake; 
ndipo wamdinda (Chidindo) 
mmakutu mwake ndi mu Mtima 
mwake ndi kumuika chivindikiro 
Mmaso mwake. Choncho ndani 
Angamuongole pambuyo pa 
Mulungu? Kodi simukumbukira? 

24. Ndipo (okanira kuuka ku 
imfa) Adanena: "Kulibe (moyo 
wina) koma Moyo wathu 
womwewu wa padziko Lapansi; 
timafa ndi kukhala ndi moyo; 
Palibe chikutiononga koma nthawi 
Basi." Koma iwo alibe kudziwa pa 
Zimene akunenazo; 
akungoganizira Chabe. 

25. Ndipo aya Zathu 
zikawerengedwa Kwa iwo 
zolongosola chilichonse 
Momveka, alibe mtsutso wina 
koma Kunena kuti:"Tibweretsereni 
atate Athu (aukitseni akhale ndi 
moyo) ngati Inu muli oona!" 

26. Nena (kwa iwo iwe 
Mtumiki): "Mulungu 
amakupatsani moyo.Kenako 
Amakupatsani imfa. Kenako 
Adzakusonkhanitsani tsiku la 
Kiyama Lopanda chikaiko." Koma 
Anthu ambiri sakudziwa. 

27. Ndipo ufumu wa 
kumwamba ndi pansi Ngwa 
Mulungu, ndipo tsiku limene 















&Z8U&&&&&& 

W^a 



Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 I 1081 I t o ^\ 



i O *J\±-\ 0jj-*» 



Kiyama idzachitika, (anthu) 
ogwirizana Ndi zonama 
adzaonongeka patsikulo. 

28. Ndipo udzaliona gulu 
lililonse Litagwada (uku nkhope 
zili zyoli); Gulu lililonse 
lidzaitanidwa ku Kaundula wake 
(kukamuwerenga): "Lero 
mulipidwa zimene mudali Kuchita!" 

29. Uyu kaundula wathu 
akunena zoona Za inu; ndithu, Ife 
tidali kulemba Zimene mudali 
kuchita." 

30. Koma amene adakhulupirira 
ndi kuchita Zabwino, Mbuye 
wawo adzawalowetsa Ku chifundo 
Chake; kumeneko Ndiko 
kupambana koonekera. 

31. Ndipo amene adakanira, 
(adzauzidwa Kuti): "Kodi aya 
Zanga sizidali Kuwerengedwa kwa 
inu? Koma inu Mudadzikweza; 
ndipo mudali anthu Oipa. 

32. Ndipo kukanenedwa kuti 
lonjezo la Mulungu ndiloona, 
ndikuti Kiyama ilibe chikaiko, 
mudali kunena, 'Sitikudziwa 
Kiyama kuti nchiyani; 
Tikungoganizira chabe, ndipo tilibe 
Chitsimikizo (za Kiyamayo)'" 

33. Choncho, kuipa kwa zimene 
adachita Kudzawaonekera, ndipo 
Zidzawazinga zimene ankazichitira 
Chipongwe. 















Surat 45. Al-Jathiyah Juzu 25 



1082 



lo *jJH 



i O UUrl djj-» 



34. Kudzanenedwanso kwa 
iwowa: "Lero Tikuiwalani 
(pokusiyani mchilango) Monga 
momwe inu mudaiwalira 
kukumana Ndi tsiku lanu ili. Ndipo 
malo anu ndi Kumoto, ndipo 
mulibe wokupulumutsani. 

35. Zimenezi nchifukwa chakuti 
inu Mudazichitira chipongwe aya 
za Mulungu, Ndipo moyo wa pa 
dziko udakunyengani." Choncho 
lero satulutsidwa mmenemo Ndipo 
madandaulo awo Savomerezedwa. 

36. Choncho mbiri zonse 
zabwino nza Mulungu, Mbuye 
wakumwamba ndi Mbuye wa 
padziko lapansi; Mbuye 
Wazolengedwa. 

37. Ndipo ukulu ndi Wake, 
kumwamba ndi Pansi; ndipo lye 
ndi Wamphamvu zoposa, Wanzeru 
zakuya! 



















Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 I 1083 I f\^i in Jifc-ty 5^ 




SURAT AL-AHQAF XL VI 




Surayi nkhani yake ikufotokoza zakutsika kwa Qur'an 
kuchokera kwa Mulungu ndi kuti nkofunika kuikhulupirira, ndi 
kumkhulupirira Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale ndi 
iye) ndi kukhulupiriranso tsiku lomaliza. Ndipo yatilimbikitsa 
kulingalira zovuta zimene zidawapeza anthu akale amene 
amanyoza Chauta pamodzi ndi aneneri Ake. Ndipo ikutiuza 
kuika mtima pochitira zabwino makolo awiri (mayi ndi bambo). 
Yafotokozanso nkhani ya kagulu ka ziwanda (majini) zimene 
zidamvetsera Qur'an ndi kulangizana pakati pawo kumvetsera 
mwachete. Ndipo zidaipeza ikuchitira umboni zimene adadza 
nazo aneneri akale; ikuongolera ku ehoona ndi njira yolunjika, 
ndipo zidaikhulupirira. Kenako zidaitanira ziwanda zinzawo 
kuchikhulupirirocho . 

Surayi yamaliza ndi nkhani yolangiza Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale ndi iye) kuti apirire pakukanidwa ndi anthu 
ake ndikuti atsanzire atumiki anzake akale pakupirira masautso. 




Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 I 1084 I tu>i 1 1 «Jlfc-ty 5j^ 



SuratAl-AhqafXLVI 



w,- w 



mm^:: *' 



j 



;« : 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Hd-Mim. 

2. Chivumbulutso cha Bukuli 
nchochokera Kwa Mulungu 
Wamphamvu zoposa, Wanzeru 
zakuya. 

3. Sitidangolenga thambo ndi 
nthaka Ndiponso zonse zapakati pa 
izo Koma mwachoonadi ndi 
nyengo yoikidwa 
(Yodziwika).Koma amene akana 
Kukhulupirira (Mulungu) 
Ngonyozera zimene achenjezedwa. 

4. Nena: Tandiuzani amene 
Mukuwapembedza ndi kumsiya 
Mulungu, ndisonyezeni chimene 
Adalenga panthaka? Kapena ali 
ndi Gawo la kuthangata polenga 
thambo? Ndibweretsereni Buku 
limene lidadza Kale, ili lisanadze, 
kapena zizindikiro Zanzeru, ngati 
inu mukunena zoona. 

5. Kodi ndani wasokera 
kwambiri kuposa Amene 
akupembedza zina kusiya Mulungu 
Zomwe sizingathe kumuyankha 
mpaka Tsiku la chiweruzo ndipo 
izo (zimafano) Sizikuzindikira za 
mapemphero awo. 



oju£\<&&\&\j 



— <w 



®i 















Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 I 1085 I t n *>» f\ <Jifc*ty Sjj- 



6. Ndipo anthu onse 
Akadzasonkhanitsidwa Adzakhala 
adani awo ndikuwakanira 
Mapemphero awo. 

7. Ndipo pamene 
zikuwerengedwa kwa iwo Aya 
Zathu zolongosola chilichonse 
(cha M'chipembedzo), amene 
Sadakhulupirire amanena pa 
choonadi Chikawadzera: "Awa ndi 
matsenga Oonekera". 

8. Kapena akunena kuti: 
"Waipeka (Qur'an)?Nena: "Ngati 
ine ndaipeka, Ndipo simungapeze 
chondithandizira Nacho kwa 
Mulungu (ku chilango Chake)". 
lye ndiwodziwa kwambiri Zimene 
mukuzijijirikira. lye Akukwana 
kukhala mboni pakati pa ine Ndi 
inu ndipo lye Ngokhululuka 
Kwabasi, Wachisoni. 

9. Nena: "Ine sindine woyamba 
pa aneneri, Ndipo sindikudziwa 
zimene zidzachitike Kwa ine 
ngakhale kwa inu. Sinditsatira 
Koma zokhazo zimene 
zikuvumbulutsidwa Kwa ine; 
ndipo ine sindili kanthu koma 
Mchenjezi wolongosola 
(Zofunika)". 

10. Nena: "Tandiuzani, ngati 
(Buku ili) Litachokera kwa 
Mulungu, ndipo inu Nkulikana uku 
mboni yochokera mu Ana a Israeli 





















Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 



1086 



n ^jJt-i t% uiu^Si 5j>* 



itachitira umboni kuti Idaliona 
longa limeneli, ndipo iwo 
Nkulikhulupirira (Bukuli) pomwe 
inu Mwadzitukumula, ndithu, 
Mulungu Saongola anthu 
osalungama. 

11. Ndipo amene 
sadakhulupirire adanena Kwa 
amene adakhulupirira: 
"(Chipembedzo ichi) chikadakhala 
Chabwino, awa sakadakhala 
otsogola ku Chimenechi pa ife." 
Ndipo chifukwa Choti sadaongoke 
nalo (Bukuli), akhala Akunena: 
"Hi ndi bodza lakale." 

12. Ndipo lisadadze ili lidalipo 
Buku la Musa monga mtsogoleri 
Ndi chifundo. Ndipo Buku ili 
likuikira Umboni (za Bukulo) 
m'chiyankhulo cha Chiarabu kuti 
liwachenjeze amene Adzichitira 
okha chinyengo, ndi kuti Likhale 
uthenga wabwino kwa ochita 
Zabwino. 

13. Ndithu, amene anena (kuti): 
"Mbuye Wathu ndi Mulungu". 
Kenako Ndikulungama, 
sadzakhala ndi Mantha (tsiku 
lakufa kwawo ngakhale Pambuyo 
pake), ndiponso Sadzadandaula. 

14. Iwo wo ndi wo anthu aku 
Jannat Adzakhala kumeneko 
Muyaya kukhala mphoto ya 
Zimene amachita. 






''* 















Surat 46. AI-Ahqaf Juzu 26 



1087 



Y 1 *j*-l in iJlfc-ty 5jj~- 



15. Ndipo tamulangiza munthu 
kuchitira zabwino Makolo ake. 
Mayi wake adatenga Pathupi pake 
mwamasautso; ndipo Adam'bala 
mwamasautso. Kutenga Pakati 
pake ndi kumsiitsa kuyamwa Ndi 
miyezi makumi atatu. Kufikira 
Atakula msimkhu nkukwana zaka 
Makumi anayi, (akakhala mwana 
Wabwino) amanena: "O, Mbuye 
wanga! Ndilimbikitseni kuthokoza 
mtendere Warm umene 
mwandipatsa pamodzi ndi Makolo 
anga, ndipo ndilimbitseni kuti 
Ndizichita zabwino zimene (Inu) 
Muziyanja ndipo ndikonzereni ndi 
Kundilungamitsira ana anga. Ine 
Ndatembenukira kwa Inu; 
ndiponso Ine ndine m'modzi mwa 
ogonjera (Inu)." 

16. Iwowo ndiamene 
tikuwalandira Zabwino zimene 
adachita ndipo Tikuwakhululukira 
zolakwa zawo. Adzakhala m'gulu 
la anthu a ku Jannat. Hi ndi lonjezo 
loona lorn we Adalonjezedwa. 

17. Tsono (mwana woipa) 
amene akunena Kwa makolo ake, 
(akamuitanira ku Chikhulupiriro 
kuti) "Ndithu ndinu Oipa (pa 
zimene mukundiitanirazi)! 
Mukundilonjeza kuti 
ndidzatulutsidwa Mmanda ndili 
wamoyo, chikhalirecho Mibadwo 
ndi mibadwo idapita Kumanda ine 



>i* 









Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 



1088 



Yn ^jA-l i*\ uJtf^Sl ijy* 



kulibe (koma mpaka lero 
Siidauke)?" Ndipo uku makolo ake 
Akupempha Mulungu kuti 
Ampulumutse ndi kumuongola ndi 
Kunena kwa iye: "Tsoka kwa iwe 
Khulupirira (Mulungu ndi kuuka 
ku Imfa, ngati sutero 
waonongeka). Ndithu, Lonjezo la 
Mulungu ndiloona." Koma Iye 
nkumanena (kuti): "Sikanthu izi 
Mukuzinena koma ndi nthano Za 
anthu akale." 

18. Iwowo ndiamene 
latsimikizika pa iwo Liwu (la 
chilango) pamodzi ndi Mibadwo 
ya ziwanda ndi anthu, imene 
Idanka kale iwo kulibe; ndithu, 
iwo Adali otaika. 

19. Ndipo aliyense 
wokhulupirira Adzakhala ndi 
nyota molingana ndi Zimene 
adachita, ndi kuti (Mulungu) 
Awalipire zochita zawo ndipo iwo 
Sadzaponderezedwa. 

20. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
limene Adzaikidwa pafupi ndi 
moto amene Sadakhulupirire 
(adzawauza kuti) "Mudaononga 
zabwino zanu mmoyo Wadziko 
lapansi, (choncho lero 
Simuzipezanso),ndipo inu 
mudasangalala Nazo zimenezo, 
choncho lero Mupatsidwa chilango 
chokusambulani Chifukwa cha 
kudzikweza kwanu Padziko 









Surat 46. AI-Ahqaf Juzu 26 



1089 



n *>i t n <Ji&*ty s^ 



popanda choona, ndiponso 
Chifukwa cha kulakwa kwanu." 

21. Ndipo kumbuka za m'bale 
wa Adi, (Mtumiki Hud) pamene 
adachenjeza Anthu ake kudziko la 
milu ya Mchenga. Ndithu, 
adaliponso achenjezi lye asadadze 
ndiponso iye atapita. (lye 
adawauza anthu ake): 
"Musampembedze aliyense koma 
Mulungu; ndithu ine 
ndikukuoperani Chilango cha tsiku 
lalikulu." 1 

22. Adanena: "Ha! Kodi 
watidzera kuti Utipatule ku 
milungu yathu? Choncho 
Tibweretsere zimene 
ukutilonjezazo Ngati uli mwa 
Onena zoona." 

23. Adanena (Hud): "Ndithu 
kudziwa (Kwenikweni kwa 
zimenezo) kuli kwa Mulungu; 
ndipo ine ndikungofikitsa Kwa inu 
zimene ndatumidwa koma ine 
Ndikukuonani kuti inu ndinu anthu 
Amene mukuchita (zinthu za) 
umbuli!. 

24. Kenako pamene adauona 
mtambo Ukulunjika ku zigwa 
zawo, adanena, "Mtambo uwu ndi 
wotivumbwitsira Mvula!" 
(Adauzidwa): "Iyayi, Chimenechi 

1 Dziko la milu ya mchenga: Awa ndi malo 
mzinda wa Hadhwara Mauti pakati pa dziko la 



\jo^x>y>\ teK?** As^i^ 












omwe akupezeka kummwera kwa 
Omman ndi Yemen kwao kwa Adi. 



Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 



1090 



Yn frjJH tnJu^is^ 



ndichimene Mudachifulumizitsa 
chija (kuti chidze Mwachangu!) 
Mphepo (ya mkutho) Yomwe 
mkati mwake muli chilango 
Chowawa! 

25. Yoononga chinthu 
chilichonse mwa Lamulo la Mbuye 
wake!" Kenako adali 
Osaonedwanso, kupatula nyumba 
zawo (Ndizimene zidatsalira). 
Umo Ndim'mene timawalipirira 
anthu oipa. 

26. Ndipo ndithu, tidawapatsa 
mphamvu Yochitira zinthu ndi 
kukhala ndi chuma Chambiri ndi 
moyo wautali zomwe 
Sitidakupatseni inu (Akuraishi) 
ndipo Tidawapatsa makutu ndi 
maso ndi Mitima,koma makutu 
awo ndi maso Awo ndi mitima 
yawo sizidawapindulire 
Chilichonse chifukwa chotsutsa 
aya za Mulungu; ndipo 
zidawazinga zomwe Adali 
kuzichitira chipongwe. 

27. Ndithu, tidaiononga midzi 
imene Yakuzungulirani; ndipo 
Tidawafotokozera momveka aya 
Zathu Kuti abwerere. 

28. Chifukwa chiyani 
siidawapulumutse Milungu imene 
adaipangayo kusiya Mulungu kuti 
iwayandikitse kwa lye (Mulungu)? 
Koma idasoweka kwa iwo (Pomwe 















Surat 46. AI-Ahqaf Juzu 26 



1091 



Y*\ s.jA-1 t % <Jlfc*ty Sjj- 



iwo adali pamavuto ofuna 
Kulandira chithandizo). Ndipo 
Zimenezo ndizo zotsatira zabodza 
lawo Ndi zomwe adali kupeka. 

29. Ndipo (kumbuka iwe 
Mtumiki{SAW}) Pamene 
tidakutumizira gulu la ziwanda 
(Majini) kudzamvera Qur'an ndipo 
pamene Izo zidafika pamalopo 
zidanena pakati Pawo: "Khalani 
chete!" Pomwe Kuwerenga (kwa 
Qur'an) kudatha, Zidabwerera ku 
mtundu wawo Kukawachenjeza 
(za chilango cha Mulungu). 

30. Zidanena: "E, inu anzathu! 
Ife tamva (Zowerengedwa) za 
m'buku (Lolemekezeka) lomwe 
Lavumbulutsidwa pambuyo pa 
Musa, Loikira umboni zimene 
Zidalitsogolera; likuongolera ku 
choona Ndi kunjira yolunjika". 

31. "E, inu anzathu! 
Muvomereni woitana Wa 
Mulungu, ndipo mkhulupirireni; 
(Mulungu) akukhululukirani 
machimo Anu ndi kukutetezani ku 
chilango Chowawa. 

32. Ngati wina samuvomera 
woitanira Kwa Mulungu, 
sangamulepheretse (Mulungu) 
padziko (akafuna kumuchita 
Kanthu), ndipo iye alibe atetezi 
ena Kupatula Iye (Mulungu). Otere 
akusokera Koonekera poyera." 















Surat 46. Al-Ahqaf Juzu 26 



1092 



Y 1 *>■» 1 1 <Jlfc^|l 5^ 



33. Kodi iwo saona kuti 
Mulungu Amene Adalenga thambo 
ndi nthaka, ndipo Sadatope 
pozilenga, ndi Wakutha 
Kuwaukitsa anthu ku imfa? Inde, 
ndithu lye Ngokhoza kuchita 
chilichonse 

34. Ndipo (akumbutse za) tsiku 
limene Adzaperekedwa ku moto 
amene Sadakhulupirire (uku 
akuuzidwa): "Kodi izi sizoona?" 
Adzanena: "Inde, Pali Mbuye 
wathu !" (Mulungu) adzanena: 
"Choncho, Lawani chilango 
chifukwa cha kukana (Choonadi) 
kwanu." 

35. Choncho pirira 
(Mtumiki{SAW}) monga 
Adapirira aneneri, eni mphamvu 
ndi Kulimba pa chipembedzo, 
(monga Nuh, Ibrahimu, Musa ndi 
Isa); ndipo Usawachitire changu. 
Tsiku limene Adzaziona zimene 
adalonjezedwa Kudzakhala monga 
iwo sadakhalitse Padziko koma 
ngati adakhala ola Limodzi lokha 
lamasana. (Zomwe 
Mukuuzidwazi) ndi ulaliki 
okwana. Palibe adzaonongedwe 
(ndi Chilango cha Mulungu), 
kupatula anthu Ochimwa (otuluka 
m'chilamulo cha Mulungu). 












Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1093 



y\ tjk-\ 



i v ju^ a jj-- 




SURAT MUHAMMAD XL VII 




Surayi yalongosola kumayambiriro kwake, kuti ndithu, 
Mulungu adaononga zochita za osakhulupirira chifukwa cha 
kutsata zonama kwawo. Ndipo wawafafanizira okhulupirira 
machimo awo chifukwa chotsatira zoona. 

Yafotokozanso mwatsatanetsatane kuti kuteteza choona 
nkofunika; kutinso mphoto ya ntchito imeneyo, pa tsiku 
lomaliza, ndi kulowa ku mtendere. Ndipo yawalimbikitsa 
okhulupirira kuti achipulumutse chipembedzo cha Mulungu, ndi 
kumenya nkhondo panjira yake. Kenako yafotokozanso kuti 
anthu achinyengo, akapatuka pa chikhulupiriro, amaononga ndi 
kuthetsa chibale padziko. 

Ndipo yachenjeza za a chinyengo kuti anthu oterewa 
asakhale pakati pa anthu okhulupirira, chifukwa iwo samvera 
mawu a Mulungu kuti awalimbikitse mtima, koma okonda 
ukazitape basi. Ndipo yawaopseza achinyengo kuti Mulungu 
aulula za kaduka kawo komwe kali m'mitima mwawo kwa 
Mtumiki Wake. 

Surayi yaletsa Asilamu kufooka pankhondo yolimbana ndi 
anthu osakhulupirira pomwe iwo ngapamwamba ndikutinso 
Mulungu ali nawo pamodzi. Ndipo sadzawachepetsera mphoto 
yantchito zawo. 




Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1094 



rn *>i 



£ V JU£ 5 j j** 



Surat Muhammad XL VII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Amene adam'kana (Mulungu 
ndi Mthenga Wake) ndi 
kutsekereza anthu Kuyenda panjira 
ya Mulungu (Powaletsa kulowa 
m'Chisilamu), Mulungu waononga 
zonse zabwino Zimene adachita . 

2. Ndipo amene akhulupirira 
nkumachita Zabwino, 
nkuzikhulupirira zimene 
Zavumbulutsidwa kwa 
Muhammad(SAW), Zimene zili 
zoona zochokera kwa Mbuye 
wawo, wawafafanizira zolakwa 
Zawo, ndipo awakonzera 
chikhalidwe Chawo (patsiku 
lomaliza ndi padziko Lapansi). 

3. Zimenezi nchifukwa chakuti 
amene Sadakhulupirire adatsata 
chonama, Ndipo amene 
adakhulupirira adatsatira Choonadi 
chochokera kwa Mbuye wawo. 
M'menemu ndim'mene Mulungu 
Akulongosolera kwa anthu 
Pamakhalidwe awo (kuti alingalire 
ndi Kupeza phunziro). 

4. Mukamakumana nawo 
pankhondo Amene sanakhulupirire 
amenyeni Makosi awo (aduleni), 
mpaka Mwafooketse pochuluka 



w. 



.-1 \&&Ste , 



oj&3\^%&\j 



-& 















Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1095 



yi *>i 



l V >U£ 6jj~t 



ophedwa Mwa iwo; kenako 
amangeni ndi Zingwe (otsalawo). 
Ngati mutafuna Kuwamasula 
popanda dipo kapena kuti apereke 
Dipo, (zili kwa inu).Kufikira 
nkhondo itatha. Limenelo ndi 
lamulo la Mulungu. Ndithu, 
Mulungu akadafuna akadathana 
nawo lye mwini powaononga onse 
psiti; Koma (wakulamulani kuti 
muchite Nkhondo) ncholinga choti 
awayese mayeso ena Ainu pa ena 
(okhulupirira pa okanitsitsawo). 
Ndipo amene aphedwa panjira ya 
Mulungu, ntchito yawo 
sadzaipititsa Pachabe. 

5. Awaongolera (ku zimene 
Zingawapindulitse pa dziko 
lapansi Ndi patsiku lomaliza) ndi 
kuwakonzera Zinthu zawo ndi 
chikhalidwe chawo, 

6. Ndi kukawalowetsa ku Munda 
wa Mtendere umene Adawadziwitsa. 

7. E, inu amene 
mwakhulupirira! Ngati Muteteza 
chipembedzo cha 
Mulungu,(Mulungu) 
adzakutetezani (Kwa adani anu) 
ndi kulimbikitsa Mapazi anu 
(pankhondo). 

8. Koma amene akana 
(Mulungu ndi Aya Zake) 
kuwonongeka nkwawo Ndipo 
awaonongera zochita zawo. 






ty$K7^Z$>£i* 



©. 



ox&qm 



u5j 









Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1096 | tl ^j*-i 



i V ju^ «j j-- 



9. Zimenezo nchifukwa chakuti 
iwo Azida zomwe Mulungu 
adavumbulutsa (Monga Qur'an ndi 
malamulo ake;) Choncho 
waziononga Zochita zawo. 

10. Kodi sadayendeyende 
padziko nkuona Kuti adali bwanji 
mapeto a amene Adawatsogolera 
(monga Adi ndi Samudi, ndi anthu 
a Luti ndi ena Otero)? Mulungu 
adawaononga psiti, Ndipo chilango 
ngati chimenecho Chidzakhalanso 
kwa osakhulupirira. 

11. Zimenezo nchifukwa 
chakuti Mulungu Ndi Mtetezi wa 
amene akhulupirira, Koma 
osakhulupirira alibe mtetezi. 

12. Ndithu, Mulungu 
adzawalowetsa ku Minda ya 
mtendere amene Adakhulupirira 
ndi kuchita zabwino, (Momwe) 
pansi pake ikuyenda Mitsinje; 
koma amene sadakhulupirire 
Akusangalala (padziko lapansi) ndi 
Kudya momwe zidyera ziweto 
(Popanda lingaliro lililonse 
kupatula Lingaliro la mimba zawo 
ndi Kukwaniritsa zilakolako za 
Chilengedwe chawo); Ndipo Moto 
ndi wo malo awo. 

13. Ndi ambiri mwa eni 
mizinda (yakale) omwe Adali 
amphamvu kuposa eni mzinda 
Wakowu umene akutulutsamo (eni 









©*us&3# 






Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1097 



Tl *>l 



t V -U* Sj j~- 



ake,) Tidawaononga (ndi zilango 
Zosiyanasiyana) koma padalibe 
Wowateteza (kwa Ife). 

14. Kodi angafanane, (polandira 
mphoto,) Amene ali ndi umboni 
wodziwika wochokera Kwa 
Mbuye wake, (kotero kuti 
Nkumamumvera, ndi amene 
Wakometsedwa ndi zochita zake 
zoipa Natsatira zilakolako zawo. 

15. Fanizo la Munda wa 
mtendere (Janna) Umene 
alonjezedwa oopa Mulungu 
(Potsatira malamulo Ake ndi 
kusiya Zoletsedwa, udzakhala 
chonchi): M'menemo muli 
mitsinje yamadzi Osasintha fungo 
lake; ndi mitsinje Yamkaka 
wosasasa mkakomedwe kake; Ndi 
mitsinje yavinyo wokoma Kwa 
akumwa ndi mitsinje ya uchi 
Woyeretsedwa (kuphula), ndiponso 
Iwo adzapeza m'menemo mtundu 
Uliwonse wazipatso ndi 
chikhululuko Chochokera kwa 
Mbuye wawo. Angafanane ndi 
wokhala muyaya Kumoto, ndi 
kumwetsedwa madzi Owira omwe 
akadula matumbo awo? 

16. Ndipo ena mwa iwo (okana 
Mulungu) Amamvetsera kwa iwe, 
(popanda Kupindula chilichonse), 
ndipo Akachoka pamalo pakopo, 
amanena Kwa amene apatsidwa 
nzeru (mwa Omtsatira ake): "Kodi 















Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1098 



n fj*-» 



£ V *W£ 5 j j-*» 



(Mtumiki) Wanena chiyani 
posachedwapa?" Iwowo Ndiamene 
Mulungu wawadinda M'mitima 
mwawo (ndi chidindo Chokana 
Mulungu), ndipo amatsatira 
Zilakolako zawo (zachabe). 

17. Ndipo amene aongoka, 
(Mulungu) Amawaonjezera 
chiongoko ndi Kuwapatsa kuopa 
kwawo (Komuopa Mulungu). 

18. Palibe chimene 
akuyembekezera tsiku 
Lachiweruziro limene liwadzere 
Mwadzidzidzi (uku iwo ali 
otanganidwa Ndi zam'dziko)? 
Ndithu zizindikiro zake Zadza 
kale; kodi kudzawapindulira 
chiyani Kukumbuka kwawo 
likadzawadzera (Tsikulo)? 

19. Dziwa kuti palibe 
wompembedza M'choonadi koma 
Mulungu, ndipo Pempha 
chikhululuko pa zolakwa zako Ndi 
zolakwa za okhulupirira achimuna 
ndi Achikazi; ndipo Mulungu 
akudziwa malo Anu opita ndi 
kubwera ndi malo anu 
Wokhazikika. 

20. Ndipo amene akhulupirira 
akunena (Chifukwa cha mazunzo 
omwe Amawapeza kuchokera kwa 
Osakhulupirira kuti) kodi 
nchifukwaNinji 
siikuvumbulutsidwa sura 



9 ? £\<* ** *Z'\<\ 9 'C 9 L"'>4i' 












Siirat 47. Muhammad Juzu 26 



1099 



y*\ *j*-i 



t V JU^ o jj-» 



(Yotiloleza kumenyana ndi 
Osakhulupirira Mulungu amene 
Akutiputa)? Koma 
ikavumbulutsidwa Sura 
yokhazikika (lamulo lake),ndipo 
Mkati mwake ndi kutchulidwa 
nkhani Zankhondo, uwaona amene 
ali ndi Matenda m'mitima mwawo 
Akukuyang'ana m'mayang'anidwe 
a Yemwe akukomoka ndi imfa, 
(chifukwa Cha kulida lamulo 
lomenyana ndi Osakhulupirira), 
basi kuonongeka ndi Kwawo. 

21. (Zofunika ndi) kumvera ndi 
mawu Abwino ndi kuti chinthu 
Chikatsimikizika (achichite). Ngati 
Akadamvera Mulungu, ndithu 
zikadakhala Zabwino kwa iwo. 

22. Mwina mwake inu 
mukanyoza (Chisilamu), 
mubwerera m'mbuyo ku Zomwe 
mudali nazo (m'nthawi ya Umbuli) 
monga kuononga padziko Ndi 
machimo) ndi kudula chibale chanu. 

23. Oterewo ndiamene 
Mulungu Wawatemberera ndi 
kuwagonthetsa Ndi kuwachititsa 
khungu maso awo. 

24. Kodi sakuilingalira Qur'an? 
Kapena m'mitima mwawo 
M'motsekedwa ndi maloko ake? 

25. Ndithu, amene akubwerera 
m'mbuyo (Kusiya chipembedzo 
chawo Nkubwerera ku 



^5ift£Jt 






\\ 9 > Z J ~ 9< 9 l9*'£ 9, 9 l9,s \'< 









Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1100 



tn *>i 



£ V *U* 5 j j-» 



zosakhulupirira Mulungu) 
chiongoko chitawaonekera Poyera 
Satana ndiamene wawanyenga, 
Ndipo Mulungu akuwapatsa nthawi. 

26. Zimenezo nkaamba kakuti 
iwo adanena Kwa omwe amada 
zimene Mulungu Wavumbulutsa 
(kuti): "Tidzakumverani M'zinthu 
zina (zimene mukutsutsana Ndi 
Mtumiki{SAW})" Ndipo Mulungu 
Akudziwa zobisika zawo. 

27. Kodi adzakhala bwanji 
pamene Angelo Azidzatenga 
mizimu yawo uku Akumenya 
nkhope zawo ndi misana Yawo? 

28. Zimenezi (imfa yoopsayi) 
nkaamba Kakuti iwo adatsata 
zomwe zidakwiitsa Mulungu ndi 
kuda zomusangalatsa (Mulungu); 
choncho adaziwononga Zochita 
zawo. 

29. Kodi amene ali ndi matenda 
m'mitima Mwawo akuganiza kuti 
Mulungu Sangaonetsere poyera 
kaduka kawo? 

30. Ndipo tikadafuna 
tikadakuonetsa iwo (Amene 
akuchitira kaduka Chisilamu) 
Ndipo ukadawadziwa ndi 
zizindikiro Zawo. Koma ndithu, 
uwadziwa M'kayankhulidwe 
(kawo) kokometsa Ndipo Mulungu 
akudziwa zochita Zanu zonse. 



®#$; 












Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1101 "*>» 



tv 



d J>-» 



31. Ndipo ndithu tikuyesani 
mayeso mpaka Tiwaonetsere 
poyera (adziwike) amene 
Akumenya nkhondo mwa inu 
(Chifukwa cha dini) ndi opirira 
(Pamavuto); ndi kuzionetsera 
poyera Nkhani zanu (zochita zanu). 

32. Ndithu,amene akana 
(Mtumiki{SAW})Ndi 
kuwatsekereza anthu kunjira ya 
Mulungu, ndi kutsutsana ndi 
Mtumiki Chiongoko chitadziwika 
kwa iwo, Sangamsautse Mulungu 
ndi chilichonse, Koma 
adzawaonongera ntchito Zawo. 

33. E, inu amene 
mwakhulupirira! Mverani 
Mulungu ndiponso mverani 
mtumiki (Wake) ndipo 
musaononge zochita zanu. 

34. Ndithu, amene 
sadakhulupirire ndi Kwatsekereza 
anthu kunjira ya Mulungu, kenako 
nkufa uku ali Osakhulupirira 
Mulungu Sadzawakhululukira 
(zolakwa zawo). 

35. Musafooke ndi kufuna 
chimvano, (Koma menyanani ndi 
adani anu); inu Ndinu opambana. 
Ndipo Mulungu ali nanu 
(Pokuthangatani ndi 
kukupulumutsani,) Ndipo 
sakuchepetserani (mphoto ya) 
Ntchito zanu. 


















Surat 47. Muhammad Juzu 26 



1102 



n *>i 



£ V *U£ dj j-j 



36. Ndithu, moyo wapadziko 
ndi masewero Ndiponso ndi 
wachabechabe. Ndipo Ngati 
mukhulupirira ndi kudzipatula 
Kumachimo (Mulungu) akupatsani 
Malipiro anu, ndipo 
sakukupemphani Chuma chanu. 

37. Ngati akadachifuna 
(kuchokera) kwa inu Chumacho 
ndi kukuchulukitsirani 
(Chopereka),mukadachita 
umbombo (Ndi chumacho), ndipo 
akadatulutsira (Poyera) kaduka 
kanu. 

38. Ha! Ndinu amene 
mukuitanidwa kuti Mupereke 
(chuma) munjira ya Mulungu. 
Koma alipo ena a inu akuumira 
Ndipo amene akuumira akuzimana 
yekha. Mulungu 

Ngwachikwanekwane ndipo inu 
Ndinu amphawi .Ngati munyoza 
(Chisilamu) Ndi kubwerera 
m'mbuyo posakhulupirira) 
Mulungu adzabweretsa m'malo 
mwanu Anthu ena; iwo sadzakhala 
ngati inu. 






®$g\ 










Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1103 



TltjJt-t tAj^lSj^ 




Surayi koyambirira kwake ikufotokoza za kupambana 
kwakukulu kumene Mulungu adamukonzera Mtumiki Wake 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndi zotsatira zikuluzikulu 
m'kufala kwa Chisilamu, ndi Asilamu kukhala ndi mphamvu, 
ndiponso m'mene Mulungu adalimbikitsira okhulupirira mitima 
kuti chikhulupiriro chawo chiwonjezeke. 

Ikufotokozanso za chilango cha anthu achinyengo ndi 
ophatikiza Mulungu ndi mafano ndi kutinso Muhammadi 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) adatumizidwa kuti akhale 
mboni ndi kulengeza nkhani yabwino kuti anthu akhulupirire 
mwa Mulungu. Ndipo kenako Surayi yafotokoza za malonjezo a 
anthu oona omwe adalonjezana ndi Mtumiki kupita ku nkhondo 
pachifukwa chakuti ankaganizira kuti Mulungu sakampulumutsa. 

Yafotokozanso za kufuna kwawo kutuluka kupita ku 
nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale 
naye) ncholinga chokapeza chuma chosiyidwa ndi adani. Ndipo 
kenako yafotokozanso kuti iwo adzaitanidwa kuti akamenyane 
ndi anthu amphamvu, ndipo yanenetsa kuti palibe uchimo 
kusapita kunkhondo ngati pali zifukwa zomveka. 

Kenako yafotokoza za kukula kwa mphoto ya omwe 
adam'lonjeza Chauta pa lonjezo la Rizuwani. Ndipo 
yafotokozanso kuti osakhulupirirawo akadayesera kumenyana 
ndi Asilamu akadathawa. Ndipo kenako yanenanso za cholinga 
cha Mulungu chanzeru powamanga manja osakhulupirira kuti 
asamenye Asilamu ndi kumanganso manja a Asilamu kuti 
asamenye osakhulupirirawo pa tsiku logonjetsa mzinda wa Makka. 

Ndipo Surayi yanenetsa kuti ndithu, Mulungu adamtsimikizira 
Mtumiki Wake zamaloto ake olowa mu Msikiti wopatulika. Ndi 
kuti Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye) pamodzi 
ndi omtsatira adali a mphamvu kwa anthu osakhulupirira Chauta. 



Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1104 



ti *>i 



1A jaflJl 0jj-*> 



I wo wokha Asilamu adali kuchitirana chifundo pakati pawo. 

Choncho m'surayi Mulungu akumuuza Mneneri Wake 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti ampatsa kupambana 
kwakukulu chifukwa chochita pangano limeneli. Umo ndi 
mom we zidalili; panganoli lidachititsa Asilamu kuti agonjetse 
mzinda wa Makka. Ndipo pasanathe zaka ziwiri Mzinda wonse 
wa Makka udagonjera Chisilamu, kenako chilumba chonse cha 
Arabia chidagonjera chipembedzochi. 

Pomaliza yafotokoza zizindikiro za okhulupirira (Asilamu) 
ndi makhalidwe awo amene amapezeka m'buku la Chipangano 
chakale ndi Chipangano chatsopano. Ndipo Mulungu walonjeza 
kwa okhulupirira, ochita zabwino chikhululuko ndi mphoto 
yaikulu. 




Siirat 48. Al-Fath Juzu 26 1 105 t n *>i 



t A jcuilt ijj**> 



Surat Al-Fath XLVIII 



^W.; 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndithu, takugonjetsera (iwe 
Mtumiki{SAW}mzinda wa 
Makka) Kugonjetsa kwakukulu 
koonekera Poyera; 1 

2. Kuti Mulungu 
akukhululukire zolakwa Zako 
zapatsogolo ndi zapambuyo, ndi 
Kukukwaniritsira mtendere Wake, 
ndi Kukuongolera kunjira 
yolunjika; 

3. Ndikuti Mulungu akuteteze 
ndi Chitetezo champhamvu. 

4. lye ndiamene adatsitsa 
chikhazikiko (Kudekha) m'mitima 
mwa okhulupirira Kuti awonjezera 
chikhulupiriro Pachikhulupiro 
chawo. Makamu Ankhondo 



^= 



qWUfc^^ 



-Ci 



as$sti®&$ 



*& 

>< 









1 M'chaka cha chisanu ndi chimodzi chisamukire Mtumiki(SAW), Mtumiki 

(madalitso ndi mtendere zikhale naye) adapita ku Makka kuchokera ku Madina 

pamodzi ndi omtsatira ake kuti akachite Umura imene ndi Haji yaing'ono. 

Koma atayandikira ku Makka, Akuraishi adamuletsa kulowa mumzindamo kuti 

asachite mapemphero a Umura. Ndipo atakambiranakambirana adamvana 

mfundo zingapo, zina mwa izo ndi:- 

(i) Asamenyane nthawi imeneyo. 

(ii) Abwerere ndipo adzabwere chaka chotsatiracho mwezi wonga umenewo 

kudzachita mapemphero. Panthawiyo sadzawaletsa kulowa mu mzindawo. 

(iii) Asiye kumenyana pakati pawo kwa zaka khumi, ndi kumayenderana 

m'mene angafunire; Akuraishi azipita ku Madina ngati atafuna, popanda 

kuzunzidwa. 

(iv) Mafuko ena a Arabu adaioledwa kulowa nawo m'pangano limeneli kuti 

asamthire nkhondo Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye), ndipo 

iyenso asawathire nkhondo. 



Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1106 



y\ *>» 



t A jiaJl Sjj-* 



akumwamba ndi pansi, Nga 
Mulungu, (monga Angelo, 
Ziwanda, nyama ziphaliwali, 
mphepo Yamkutho ndi zivomerezi 
ndi zina Zotero); ndipo Mulungu 
Ngodziwa Chilichonse, ndiponso 
Wanzeru zakuya; 

5. (Wachita izi) kuti okhulupirira 
achimuna Ndi achikazi 
akawalowetse m'minda Yomwe 
pansi pake ikuyenda mitsinje; 
Adzakhala muyaya m'menemo, 
Ndi kuti awafafanizire zolakwa 
zawo; Kumeneko ndiko kupambana 
Kwakukulu kwa Mulungu. 

6. Ndi kuti awalange 
achiphamaso Achimuna ndi 
achikazi ndi Omphatikiza 
Mulungu achimuna ndi Achikazi 
oganizira Mulungu maganizo 
Achabe. Kutembenuka koipa kuli 
kwa Iwo ndipo Mulungu 
wawakwiyira Ndiponso 
wawatemberera ndi Kuwakonzera 
Jahannamu.Ndipo kumeneko 
nkobwerera koipa. 

7. Ndipo magulu ankhondo 
akumwamba ndi Pansi nga 
Mulungu; ndipo Mulungu Ndi 
Wamphamvu zoposa, Wa nzeru 
Zakuya. 

8. Ndithu, takutumiza kuti 
ukhale mboni Ndi wolengeza 
nkhani zabwino Ndiponso 
mchenjezi. 



&s$ss&$& 












Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1107 



M *j*-» 



i A jsdil Sjj-u 



9. Ncholinga choti 
mumkhulupirire Mulungu ndi 
Mtumiki Wake, ndi kuti 
Mumtukule ndi kumulemekeza 
(Mtumiki) ndi kutinso 
mumtamande (Mulungu) m'mawa 
ndi madzulo. 

10. Ndithu, amene 
akukulonjeza, ndiye Kuti 
akulonjeza Mulungu. Dzanja la 
Mulungu lili pamwamba pa manja 
awo. Amene ati aswe lonjezo, ndiye 
kuti Wadziswera yekha (mavuto ali 
pa lye). Koma yemwe akwaniritse 
Zomwe adalonjeza kwa Mulungu, 
amulipira malipiro aakulu. 

11. Adzanena kwa iwe Arabu 
Am'midzi otsala (ku nkhondo, 
amene Adalibe zifukwa zomveka 
m'kutsala Kwawo): Chuma ndi 
ana athu Zidatitangwanitsa; 
choncho Tipemphereni 
chikhululuko. Akunena Ndi 
malirime awo (mawu) omwe 
M'mitima mwawo mulibe. Nena: 
"Kodi ndani angathe 
kukuthandizani Chilichonse kwa 
Mulungu ngati atafuna 
Kukupatsani masautso, kapena 
atafuna Kukupatsani zabwino? 
Koma Mulungu Akudziwa zonse 
zimene mukuchita. 

12. Koma mudali kuganiza kuti 
Mtumiki Ndi okhulupirira 
sabwereranso ku maanja Awo, 









)y^i 









Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1108 



n frj*-i 



t A jttiJi 0jj-» 



(akaphedwa konko); zimenezo 
Zidakukondweretsani m'mitima 
Mwanu,ndipo mumaganiza ganizo 
Loipa; ndipo mudali anthu 
oonongeka." 

13. Ndipo amene sakhulupirira 
Mulungu Ndi Mtumiki Wake, 
ndithu, Ife Tawakonzera okanira 
chilango chamoto Woyaka. 

14. Ndipo ufumu wakumwamba 
ndi pansi ngwa Mulungu. 
Amakhululukira amene Wamfuna 
(ngati atatembenukira kwa lye) ndi 
kumlanga amene wamfuna (Ngati 
sanatembenukire kwa lye). Ndipo 
Mulungu Ngokhululuka kwambiri 
Ngwachisoni. 

15. Otsala (kunkhondo) aja, 
mukapita Kukatenga zotola za a 
nkhondo, Adzanena: "Tilekeni 
tikutsatileni." Akufuna kuti asinthe 
mawu a Mulungu. Nena: 
"Simutitsatira! Umo ndimo 
Mulungu adanenera kale." (Apo) 
Adzanena (kuti): "Koma 
mukutichitira Dumbo." Iyayi, 
koma nzochepa zomwe Adali 
kuzindikira. 

16. Nena kwa otsala 
(kunkhondo) mwa Arabu a 
m'midzi: Mudzaitanidwa 
(kukamenyana) ndi Anthu eni 
mphamvu zaukali; Mudzamenyana 
nawo kapena adzagonja (Ndi 



*$&$&*&$&%> 



®\ 












Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1109 



r\ *>i 



i A jaiJl Sj j-*» 



kulowa m'Chisilamu). Ngati 
Mudzamvera, Mulungu 
adzakulipirani Malipiro abwino, 
koma ngati Mutembenuka monga 
mudatembenukira kale 
Adzakulangani ndi chilango 
chowawa. 

17. Palibe tchimo pa wakhungu, 
palibenso Tchimo pa olumala, 
palibenso Tchimo pa wodwala 
(atasiya kupita Kunkhondo). Ndipo 
amene angamvere Mulungu ndi 
Mtumiki Wake, Adzam'lowetsa 
m'minda momwe Mukuyenda 
mitsinje pansi pake; ndipo Amene 
anyozere, amulanga ndi Chilango 
chowawa. 

18. Ndithu, Mulungu 
adawayanja okhulupirira Pamene 
amagwirana nawe chanza pansi Pa 
mtengo pomwe amakulonjeza 
(Kuti adzamenya nkhondo mpaka 
imfa) Mulungu adadziwa zomwe 
zidali M'mitima mwawo ndipo 
adatsitsa pa Iwo kukhazikika (ndi 
kudekha;) ndipo Adawalipira 
kupambana kwapafupi. 

19. Ndipo zotola zambiri 
zapankhondo Adzazitenga; ndipo 
Mulungu Ngwamphamvu zoposa, 
Wanzeru Zakuya. 

20. Mulungu wakulonjezani 
zotola zambiri Zapankhondo 
(zomwe) mudzazitenga, Ndipo 



<&jRlg&2 


















Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1110 



tn *>» 



t A gd\ 3 j^ 



wachita changu kukupatsani izi, 
(Zinazo asanakupatseni). Ndipo 
Watsekereza manja a anthu pa inu 
(kuti Asakumenyeni). Ndi kuti 
chikhale Chisonyezo cha 
okhulupirira (amene Akudza 
pambuyo panu), ndi kuti 
Akuongolereni kunjira yolunjika. 

21. Ndi zina zimene 
simudazithe (Kuzipeza); Mulungu 
Wazidziwa. Ndipo Mulungu 
Ngokhoza chilichonse. 

22. Amene sadakhulupirire 
akadayesa Kumenyana nanu; 
akadatembenuza Misana kuthawa; 
kenako sakadapeza Mthandizi 
kapena mtetezi. 

23. Chimenecho ndicho 
chizolowezi cha Mulungu chimene 
chidapita kale, ndipo Sungapeze 
kusintha pa chizolowezi Cha 
Mulungu. 

24. Ndipo lye ndi amene 
adatsekereza Manja awo pa inu; 
ndi manja Anu pa iwo, pa chigwa 
cha Makka, atakupambanitsani pa 
iwo. Ndipo Mulungu akuona zonse 
Zimene mukuchita. 

25. Iwowo ndiamene 
sadakhulupirire, Ndipo 
adakutsekerezani kulowa 
Mu'Msikiti wopatulika pomwe 
nyama Zansembe zidangomangika 
osakafika Pamalo pake. 



%&&£!&!&£& 



^'Mfo 















Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1111 



n *>•» 



t A £SdM 6jj*i 



Kukadakhala kuti kulibe Amuna 
okhulupirira ndi akazi Okhulupirira 
omwe simudawadziwe kuti 
Mungawaponde potero inu 
Nkudzudzulidwa popanda 
kudziwa, (Mulungu akadakulolezani 
kumenyana Nawo. Koma wachita 
izi) kuti iye Amulowetse ku 
mtendere Wake amene Wamfuna. 
Akadadzipatula, Tikadawalanga 
ndi chilango chowawa, Amene 
sadakhulupirire pakati pawo. 

26. Pamene omwe 
sadakhulupirire adaika Mkwiyo 
m'mitima, mkwiyo waumbuli, 
Mulungu adatsitsa chikhazikiko 
Chake Ndi kudekha pa Mtumiki 
Wake ndi pa Okhulupirira, ndipo 
adawalimbikitsa ndi Mawu woopa 
Mulungu; ndipo adali eni Mawuwo 
ndi oyenerana nawo. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa chilichonse. 

27. Ndithu, Mulungu 
adamtsimikizira Mtumiki Wake za 
maloto ake oona: "Ndithu, inu 
mudzalowa muMsikiti Wopatulika 
mwamtendere, Mulungu Akafuna; 
mudzameta mitu ndi kuyepula 
Tsitsi lanu, simudzaopa (nthawi 
Imeneyo); ndipo Mulungu 
amadziwa Zimene simumazidziwa, 
ndipo Zisanapezeke zimenezo, 
akupatsani Kupambana kumene 
kuli pafupi. 












9? 



Surat 48. Al-Fath Juzu 26 



1112 



y-\ fr>i 



£ A jjaiJi 5jj-» 



28. lye ndiYemwe adatumiza 
Mtumiki Wake Ndi chiongoko ndi 
chipembedzo choona Kuti achiike 
pamwamba pa zipembedzo Zonse. 
Ndipo Mulungu akukwanira 
Kukhala mboni (Yake). 

29. Muhammad(SAW) ndi 
Mtumiki wa Mulungu; Ndipo 
amene ali pamodzi ndi iye 
Ngamphamvu kwa osakhulupirira 
(Mulungu), koma ngachifundo 
chambiri Pakati pawo. Uwaona 
akugwira M'maondo ndi kugwetsa 
nkhope zawo Pansi ncholinga 
chofuna zabwino za Mulungu ndi 
chikondi (Chake). Zizindikiro 
zawo zili pankhope zawo 
Zosonyeza kulambira kwawo. Hi 
ndi Fanizo lawo m'Chipangano 
chakale, Ndipo fanizo lawo 
m'Chipangano Chatsopano nkuti 
iwo ali monga mmera Womwe 
watulutsa nthambi zake; Kenako 
(nthambizo) nkuulimbitsa ndi 
Kukhala waukulu ndi kuima 
Bwinobwino ndi tsinde lake, 
Nkuwasangalatsa omwe 
adaubzala. (Choncho) zotsatira 
zake, Nkuwakwiyitsa 
osakhulupirira chifukwa Cha iwo. 
Mulungu walonjeza Chikhululuko 
ndi malipiro aakulu (kwa) Amene 
akhulupirira ndi Kuchita zabwino 
mwa iwo. 






Surat 49. AI-Hujurat Juzu 26 I 1113 I t n *j*-i £ ^ ot^jJ-i Sj^ 




Surayi yayamba ndi kuletsa okhulupirira kupititsa lamulo 
pachinthu, Mulungu ndi Mthenga Wake asanalamule, ndi 
kukweza mawu awo pamwamba pa mawu a Mtumiki (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye). Ndipo yatama amene amatsitsa 
mawu awo akakhala ndi Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye), ndi kudzudzula amene asiya miyambo yabwino 
pomaitana Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) uku 
ali kuseri kwa zipinda za nyumba ya Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye). 

Kenako yalamula Asilamu kuti azikhazikika mitima ndi 
nkhani za anthu achinyengo, ofooka pa chikhulupiriro. Ndipo 
yalamula aweruzi zimene angachite ndi magulu awiri a Asilamu 
akamenyana. Ndipo yaletsa Asilamu kuchitirana chipongwe 
pakati pawo kusambulana, ndi kuwaganizira zoipa anthu 
abwino, ndi kufufuza zolakwa zawo. Arabu a m'madera a 
m'chipululu yawaletsa kudzitama ndi chikhulupiriro pomwe 
chisadakhazikike m'mitima mwawo. 

Kenako Surayi yafotokoza za okhulupirira amene ali oona 
pachikhulupiriro. Ndipo yamaliza ndi nkhani yoletsa kumkumba 
Mtumiki wa Mulungu (madalitso ndi mtendere zikhale naye), 
chifukwa cholowa kwawo m'Chisilamu. Ndipo yafotokoza kuti 
Mulungu ndiye woyenera kuwakumba pa zabwino zimene 
wawachitira iwo powaongolera ku chikhulupiriro. 




Surat 49. Al-Hujurat Juzu 26 1114 Y 1 *jfci £ * oiyjJ-i 5^ 



Sam* Al-Hujurat XLIX 



-^ ■■^•v^>; 



0»^j 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. E, inu amene mwakhulupirira! 
Musamatsogoze (kulamula chinthu 
Chapachipembedzo kapena 
cham'dziko) Patsogolo pa (mawu 
a) Mulungu ndi Mthenga Wake. 
Ndipo muopeni Mulungu, Ndithu 
Mulungu Ngwakumva Ngodziwa. 

2. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musamakweze 
mawu anu pamwamba Pa mawu a 
Mneneri; musakweze mawu 
Pokamba naye monga momwe 
Mumayankhulira nokhanokha, 
kuopa Kuti zochita zanu 
zingaonongeke (ndi Kukhala 
zopanda mphoto) pomwe inu 
Simukuzindikira. 

3. Ndithu, amene akutsitsa 
mawu awo Pamaso pa mtumiki wa 
Mulungu, iwo Ndiamene Mulungu 
wawayeretsa Mitima yawo 
pomuopa lye; Chikhululuko ndi 
malipiro akulu Zidzakhala pa iwo. 

4. Ndithu, amene akukuitana 
(uku ali) Kuseri kwa zipinda (za 
nyumba), ambiri A iwo sazindikira. 

5. Ndipo iwo akadapirira ndi 
kuyembekeza (Kuti) mpaka 
utuluke ndi kudza kwa iwo, 



oj*&\vP&\fr\j* 



Jb 















Siirat 49. Al-Hujurat Juzu 26 



1115 



Yt ft>» 



t ^ Olj^-l Ojj-*» 



Zikadakhala zabwino kwa iwo; 
koma Mulungu Ngokhululuka 
kwabasi Ngwachisoni. 

6. E, inu amene mwakhulupirira! 
Ngati Atakudzerani munthu 
wosakhulupirika Ndi nkhani 
(iliyonse, musamuvomereze); 
Ifufuzeni (kaye) kuopa kuti 
mungachitire Anthu (mtopola) 
mwaumbuli, ndikuti 
Mungazanong'oneze bondo pa 
zomwe Mwachita. 

7. Ndipo dziwani kuti mwa inu 
muli Mtumiki wa Mulungu, 
(mumvereni iye Zimene 
akukuuzani) kukadakhala kuti Iye 
akukumverani pa zinthu zambiri 
(Zimene mukumuuza), 
mukadavutika. Koma Mulungu 
wachichita Chikhulupiriro kukhala 
chokondedwa Kwa inu ndipo 
wachikometsa M'mitima mwanu 
ndipo wakuchitani Kuti mukude 
kusakhulupirira ndi Ufasiki 
(kutuluka m'malamulo a Mulungu) 
ndi kunyoza (Mulungu.) Iwowo 
ndiwo oongoka. 

8. (Chifukwa cha) ubwino 
wochokera kwa Mulungu ndi 
mtendere (Wake, mwapeza 
Zimenezi); ndipo Mulungu 
Ngodziwa Ngwanzeru zakuya. 

9. Ndipo ngati magulu awiri 
aokhulupirira Atamenyana 
ayanjanitseni pakati pawo. Ngati 









m* 



^■^'^ozmi 






<$&&&?<£&&&$& 






Siirat 49. Al-Hujurat Juzu 26 



1116 



Tl *>i 



t ^ Olj^-l Sjj~- 



gulu limodzi mwa magulu awiriwo 
Likuchitira mtopola linalo, 
limenyeni Limene likuchita 
mtopola mpaka Libwerere ku 
lamulo la Mulungu; Ngati 
litabwerera, ayanjanitseni pakati 
Pawo mwachilungamo, ndipo 
chitani Chilungamo; ndithu, 
Mulungu amakonda Ochita 
chilungamo. 

10. Ndithu, okhulupirira onse 
ndi pachibale Choncho 
yanjanitsani pakati pa abale Anu; 
(musanyozere lamulo la 
Kuyanjanitsa) ndipo muopeni 
Mulungu Kuti akuchitireni 
chifundo. 

11. E, inuamene 
mwakhulupirira! Amuna Asanyoze 
amuna anzawo; mwina 
(Onyozedwa) nkukhala abwino 
(kwa Mulungu) kuposa iwo 
(onyoza). Nawonso akazi asanyoze 
akazi anzawo; Mwina onyozedwa 
nkukhala abwino (Kwa Mulungu) 
kuposa iwo (onyoza). Ndipo 
musatukwanizane pokumbana 
Mitundu kapena kuitanana ndi 
maina Oipa. Taonani kuipa 
kumuyitanira Munthu ndi dzina 
loti fasiki (wotuluka M'malamulo 
a Mulungu.) Atakhulupirira kale; 
ndipo amene salapa (ku zimenezi), 
iwo ndiwo (ochimwa) Odzichitira 
okha chinyengo . 









*$ ,-fe;,<v v 1,^\ '*.-fit*SK 






Surat 49. Al-Hujurat Juzu 26 | 1117 | n *>i H oiy^i 0^ 



12. E, inu amene 
mwakhulupirira! Dzipatuleni 
kwambiri kuwaganizira Zoipa 
(anthu abwino). Ndithu, 
Kuganizira (anthu) maganizo 
(oipa) Nditchimo. Ndipo 
musafufuzefufuze (Nkhani za 
anthu) ndiponso musajedane 
Pakati panu. Kodi m'modzi wa inu 
Angakonde kudya minofu ya 
m'bale Wake wakufa? 
Simungakonde zimenezo 

Ndipo muopeni Mulungu. Ndithu, 
Mulungu Ngolandira kulapa, 
Ngwachisoni. 

13. E, inu anthu! Tidakulengani 
(nonse) Kuchokera kwa mwamuna 
(m'modzi; Adamu) ndi mkazi 
(m'modzi; Hawa), Ndipo 
tidakuchitani kukhala a Mitundu 
ndi mafuko (Osiyanasiyana) kuti 
m'dziwane (basi). Ndithu, 
wolemekezeka kwambiri mwa Inu 
kwa Mulungu, ndi yemwe ali 
woopa. Ndithu Mulungu 
Ngodziwa, ndipo Ngodziwa 
kwambiri nkhani zonse. 

14. Anthu okhala m'zipululu 
adanena(kuti): "Takhulupirira". 
Nena, Simudakhulupirire 
(kwenikweni); komaNenani 
(kuti): "Tagonjera (Mulungu)" 
Ndipo mpaka pano chikhulupiriro 
Sichidalowe m'mitima mwanu 
(ndi Kukhazikika bwinobwino). 












Siirat 49. Al-Hujurat Juzu 26 ms tu>i £ * oiy-uM Sj^ 



Koma ngati Mumvera Mulungu 
ndi Mtumiki Wake, 
Sakuchepetserani chilichonse 
m'zochita Zanu. Ndithu, Mulungu 
Ngokhululuka Kwabasi, 
Ngwachifundo chambiri. 

15. Ndithu, amene ali 
okhulupirira (moona) Ndiomwe 
akhulupirira Mulungu ndi Mtumiki 
Wake, ndipo kenako nkukhala 
Osakaika, nkuchita nkhondo panjira 
ya Mulungu, ndi chuma chawo, 
ndi matupi awo, Iwowo ndiwo 
oona (pa chikhulupiriro Chawo). 

16. Nena: "Kodi 
mukumdziwitsa Mulungu Za 
chipembedzo chanu? Koma 
Chiklialirecho Mulungu akudziwa 
zonse Za kumwamba ndi za 
m'dziko lapansi. Ndipo Mulungu 
Ngodziwa chilichonse. 

17. Akukukumba iwe chifukwa 
cha kulowa Kwawo m'Chisilamu 
(ngati kuti Akuchitira ufulu). 
Nena: "Kulowa Kwanu 
m'Chisilamu musakuyese Kuti 
mwandichitira ubwino ine, koma 
Mulungu ndiAmene wakuchitirani 
ubwino Pokuongolerani ku 
chikhulupiriro, ngati Muli oona. 

18. Ndithu, Mulungu akudziwa 
zobisika za Kumwamba ndi 
zamnthaka. Ndipo Mulungu 
akuona zimene mukuchita. 






®i 



4.>ij 









^^*r^tJS»# 



0^ 






Siirat 50. Qaf 



Juzu 26 



1119 "*>i 



o • Jj OjJ-** 




Surayi, kumayambiriro kwake, ikufotokoza za kutsimikiza 
kwa uthenga wa Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye) 
ndi kutsutsa kwa osakhulupirira zakudza kwa Mthenga 
wochokera mwa iwo, ndi kusakhulupirira zakuuka ku imfa 
atasanduka fumbi. Ndipo yasonyeza zizindikiro za chilengedwe 
cha dziko lapansi ndi kumwamba zomwe zikulangiza kuti 
Mulungu sangalephere kuukitsa anthu ku imfa. 

lye ndi Amene adawalenga pomwe poyamba sadali kanthu. 
Ndipo akudziwa zomwe mitima yawo ikuwanong'oneza ndi 
kulemba zochita ndi zonena zawo m'kaundula wosungidwa 
bwino. Ndipo yanenetsa Surayi kuti kuyesayesa kwa 
osakhulupirira pa tsiku lachiweruzo kupereka madandaulo kwa 
Mulungu kuti Satana ndi amene adawasokeretsa, 
sikudzawapindulira kanthu. M'malo mwake, Satana pamodzi 
ndi iwo adzaponyedwa ku moto. Ndipo pamenepo Mulungu 
adzachitira okhulupirira ubwino powalowetsa ku Munda wa 
mtendere wamuyaya. 

Kenako Surayi yamaliza nkhani yake ndi kulamula Mtumiki 
kuti apirire ku mazunzo a osakhulupirira omwe salingalira 
zimene zidawagwera anthu amibadwo yoyamba. Ndipo 
yamulangiza kuti alimbe pa mapemphero a Mulungu, nkutinso 
iye ntchito yake ndi kukumbutsa okhulupirira, osati kukakamiza 
osakhulupirira kuti akhulupirire. 




Surat 50. Qaf 



Juzu26 1120 tn*j*-i 



% Jj 5jJ-*» 



Swraf ga/ L 



* : # : ;; : ,:. i^ii>^ .<^\# 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Qdf: Ndikulumbira Qur'an 
yolemekezekayi (Ndithu, 
mudzaukitsidwa ku imfa). 

2. Koma akudabwa chifukwa 
chowadzera Mchenjezi wochokera 
mwa iwo. Ndipo osakhulupirira 
adanena: "Ichi nchinthu 
chodabwitsa." 

3. Kodi tikadzafa ndi kukhala 
fumbi (Tidzaukanso?) Kubwerera 
kumeneko Nkwakutali kwambiri, 
(Nkosatheka)" 

4. Ndithu, tikudziwa chimene 
nthaka Ikuchepetsa m'matupi 
mwawo (Akalowa m'manda). 
Ndipo kwa Ife kuli Kaundula 
wosungidwa. 

5. Koma adatsutsa choona 
pamene Chidawadzera. Ndipo iwo 
ali m'chinthu Chosokonezeka. 

6. Kodi sawona thambo 
pamwamba pawo M'mene 
tidalimangira ndi Kulikongoletsa? 
Ndipo lilibe ming'alu. 

7. Ndipo nthaka tidaiyala; Ndi 
kuika mapiri m'menemo Ndi 
kumeretsamo m'mera Wokongola 
wamtundu uliwonse. 



o^JJl^^U- 



-2> 






^^M^M'm^ 






*• * H * 



*&$&&&&&& 



©, 






Surat 50. Qaf 



Juzu26 1121 tl*j*-i 



o • <3 ^jj- - 



8. (Kuti zimenezi zikhale) 
chotsekula Maso ndi chikumbutso 
kwa munthu Aliyense 
wotembenukira (Kwa Mulungu). 

9. Ndipo tatsitsa madzi 
odalitsidwa Kuchokera 
kumitambo, ndipo Kupyolera 
m' madzi wo, tameretsa (Mmera) 
m'minda ndi mbewu Zokololedwa; 

10. Ndi mitengo italiitali ya 
kanjedza Yokhala ndi mikoko 
yazipatso Zothonana, 

11. (Kuti chikhale) chakudya 
cha akapolo (a Mulungu); ndi 
madziwo taukitsa dziko Lakufa 
(louma). Momwemo ndimmene 
Kudzakhalira kutuluka m'manda 
(Muli moyo). 

12. Kale, iwo kulibe, adatsutsa 
anthu A Nuhi ndi eni chitsime ndi 
Asamudu. 

13. Ndi Adi, ndi Farawo ndi 
Abale a Luti, 

14. Ndi anthu a m' mitengo (ya 
Aika), ndi Anthu a Tubba; onsewo 
adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo 
Langa Lidatsimikizika (pa iwo). 

15. Kodi tidatopa nkulenga 
Koyamba? Koma iwo ali 
M'maganizo osokonezeka 
M'zakalengedwe katsopano. 

16. Ndithu tidamulenga 
munthu, ndipo Ife Tikudziwa 



<7) 9 A 9' *&\ \\.£t' 9 C 



£$m^^y& 












9] 9\'?\' ?>'J*&\" 



Surat 50. Qaf 



Juzu26 1122 *^ *>* 



o • (3 ^jj-* 1 



zimene mtima wake 
Ukumunong'oneza; ndipo Ife tili 
pafupi Ndi iye kuposa mtsempha 
wam'khosi Mwake. 

17. Pamene amalandira olandira 
Awiri (Angelo), wina amakhala 
kudzanja Lamanja, wina kudzanja 
lamanzere, 

18. Palibe chilichonse chimene 
Amayankhula koma pafupi ndi iye 
pali Mlonda amene wakonzekera 
(kulemba). 

19. Ndipo kuledzera kwa imfa 
kukam'dzera Mwa choona, 
(pamenepo adzauzidwa): "Ichi ndi 
chomwe mumachithawa chija." 

20. Ndipo lipenga 
lidzaimbidwa; limenelo Ndilo 
tsiku lamavuto (tsiku 
Lachiweruziro). 

21. Ndipo udzadza mzimu 
uliwonse Pamodzi ndi m'busa 
(wake) ndi mboni (Yake). 

22. (Adzauzidwa): "Ndithu, 
udali Wosalabadira zinthu izi; basi 
Takuvundukulira (chomwe) 
Chimakuphimba, ndipo 
kuyang'ana Kwako lero 
nkwakuthwa!" 

23. Ndipo (Mngelo) yemwe 
adali naye (Pamodzi 
ndikumalemba zochita zake) 
Adzanena (kwa Mngelo 



%&&v^&&&® 






-• >^ w x 



,*i»t^» .«: jr.tvli . t».f » - fc*i 



«QK3Mu8y%*» 






® uu£*6u&lai '<&%$b 



Surat 50. Qaf 



Juzu26 H23 m »>■! 



• (3 5jj-u 



wachilango): "Izi ndizimene 
zidakonzedwa ndi ine. 

24. Mponyeni kumoto Aliyense 
amene Wokanira wamakani. 

25. Wotsekereza zabwino, 
Wolumpha Malire, wokaika; 

26. Amene adadzipangira 
milungu ina ndi Kumphatikiza ndi 
Mulungu. Mponyeni kuchilango 
chaukali". 

27. Mnzake(satana) adzanena: 
"O, Mbuye Wathu! 
Sindidamsokeretse, Koma iye 
mwini Adali wosokera kutali 
kwambiri ndi Choonadi". 

28. (Mulungu) adzanena: 
"Musakangane kwa Ine; 
ndidakutsogozerani kale chenjezo 
(Langa)" 

29. Mawu Anga sasinthidwa 
kwa Ine, ndipo Ine siwopondereza 
Akapolo (Anga). 

30. Tsiku limene tidzaifunsa 
Jahannama: "Kodi wadzaza?" Iyo 
idzanena: "Kodi kuli Zoonjezera?" 

31. Ndipo munda wa mtendere 
Udzayandikitsidwa pafupi kwa 
oopa (Mulungu). 

32. "Izi ndizimene 
mumalonjezedwa, za Aliyense 
wotembenukira Kwa Mulungu, 
Wosunga (malamulo Ake). 



#4?$«a$ 












Surat 50. Qaf 



Juzu26 1124 TWjA-i 



o * <j <*jj-»» 



33. Amene adaopa (Mulungu), 
Wachifundo Chambiri, pomwe 
samamuona ndi maso, Ndipo 
adadza ndi mtima wotembenukira 
(Kwa lye)." 

34. (Adzauzidwa): "Uloweni 
Mwamtendere"; limeneli ndi tsiku 
Lokhazikika mpaka muyaya 

35. M'menemo adzapeza 
chilichonse (Chimene) adzafune, 
ndipo kwa Ife kuli Zoonjezera. 

36. Ndipo kodi ndi mibadwo 
Ingati tidainonga Kale iwo kulibe, 
yamphamvu kuposa Iwo? 
Adayendayenda padziko.Kodi 
Padalipo pothawira? 

37. Ndithu, m'zimenezi muli 
chikumbutso Kwa yemwe ali ndi 
mtima ndi yemwe Akutcherera 
khutu (uku) iye ali pompo (Ndi 
maganizo ake). 

38. Ndithu, tidalenga thambo 
ndi nthaka ndi Zapakati pake 
m'masiku asanu ndi Limodzi, ndipo 
sikudatikhuze kutopa Kuli konse. 

39. Choncho, pirira nazo 
zomwe akunenazo, Ndipo 
lemekeza Mbuye wako 
Pomutamanda dzuwa lisadatuluke, 
(Swala ya Subuhi), ndi (dzuwa) 
Lisadalowe, (Swala ya Asiri), 

40. Ndi gawo lausiku, (swala ya 
Magharibi Ndi Ishaa); ndiponso 






© ^!3^W#^ 



<^j©8£$$&» 









®>3PW&%$$te 



Surat 50. Qaf 



Juzu 26 



1125 



y\ *>i 



* (j ^JJ - "** 



(mulemekeze) pambuyo Pa 
mapemphero (popemphera Swala 
Za Sunna, monga Surma za 
kabuliya ndi Baadiya ndi Tahajudi). 

41. Ndipo mvetsera (za) tsiku 
limene Woitana adzaitana 
kuchokera pamalo Apafupi. 

42. Tsiku limene adzamva 
phokoso mwa Choonadi: limenelo 
ndilo tsiku Lodzatuluka (m'manda). 

43. Ndithu, Ife ndi amene 
timapereka moyo Ndi kupereka 
imfa; ndipo kobwerera Nkwathu, 

44. (Akumbutse za) tsiku 
limene nthaka Idzang'ambike kwa 
iwo Mwachangu; kusonkhanitsa 
kumeneko Nkosavuta kwa Ife. 

45. Ife tikudziwa bwino zimene 
akunena; iwe Suli 
wowakakamiza. Choncho 
mukumbutse Ndi Qur'an yemwe 
akuopa chilango Changa. 










Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 26 



1126 



t n *j*-1 O ) OUjlJUt dj^ 




Surayi yayamba ndi kulumbira kwakuti: Ndithu, kuuka ku 
imfa ndi chiweruzo zilipo popanda chikaiko. Ndipo yatsatizanso 
kulumbira kwina pa zakutsutsana kwa okana Chisilamu 
pazimene akumunenera Mneneri wa Mulungu, Muhammad 
(SAW), ndi Qur'an kuti mawu awo ngonama. 

Kenako ikuchenjeza okanawo kuipa kwa malo awo obwerera 
ndi kupereka chithunzi cha zomwe oopa Chauta awakonzera 
monga mphoto ya ntchito zabwino zimene adatsogoza akadali 
padziko lapansi. Ndipo kenaka yatiuza kuti tiganizire 
zazizindikiro za Mulungu m'dziko ndi m'moyo wathu, ndi 
zolengedwa zodabwitsa zimene zidaikidwa m'menemo, zosalala 
m'kalengedwe. 

Surayi yafotokozanso nkhani ya Ibrahim pamodzi ndi alendo 
ake angelo. Ndipo yasonyeza chikhalidwe cha mibadwo ina ndi 
chionongeko chimene chidawapeza chifukwa chakutsutsa 
aneneri awo. Kenako yasonyeza mwachidule zina mwa 
zizindikiro za Mulungu m'dziko ndi kulimbikitsa anthu kuti 
abwerere kwa Chauta ndi kuti mapemphero akhale a Mulungu 
yekha. Ndipo mapemphero ndicho cholinga cholengedwera 
ziwanda (majini) ndi anthu. 

Surayi yamaliza ndi kuchenjeza otsutsa Mneneri wa Chauta 
za chilango chonga chimene idachilandira mibadwo yakale. 




Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 26 1 1127 I T n ^jA-i o > objiJJi oj^ 



5wra/ Adh-Dhariyat LI 



: M^T&^ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira mphepo 
imene Ikubalalitsa Mitambo ya 
mvula; 

2. Ndi imene imasenza mitolo 
Yolemera (ya madzi). 

3. Ndi kuyenda (nawo 
madziwo) Mwaubwino; 

4. Ndi awo amene amagawa 
riziki (limene Mulungu amalipereka 
kwa amene Wamfuna). 

5. Ndithu, zimene 
mukulonjezedwa Nzoonadi, 
(zidzachitika); 

6. Ndipo, ndithu,malipiro (pa 
Zochita zanu) adzapezekadi. 

7. Ndikulumbirira thambo la njira 
Zake zambiri zoikidwa mwaluso, 

8. Ndithu, inu muli m'mau 
otsutsana, (Pazimene mukunena) 

9. (Kupyolera m'mawu 
amenewa) Akuchotsedwa ku icho 
(chikhulupiriro Chalonjezo loona) 
amene Adachotsedwa (ku 
chikhulupirirocho). 

10. Aonongeka abodza (amene 
akunena Za tsiku lachiweruzo 
mongoganizira.) 



o^f^jll^l*. 



^4M 



v y^ 












&&&& 



SuratSl. Adh-Dhariyat Juzu26| H28 I T1 *>-» o\ objiiii *^ 



11. Iwo amene akubira 
muumbuli, Osalabadira (za tsiku 
lomaliza). 

12. Akufunsa (mwachipongwe 
ponena kuti) "Lidzakhala liti tsiku 
lamalipiro?" 

13. (Limenelo ndi) tsiku lomwe 
iwo Adzalangidwa kumoto. 

14. (Adzawauza kuti): "Lawani 
chilango Chanu ichi chimene 
Munkachifulumizitsa (kuti 
chikufikeni). 

15. Ndithu, oopa (Mulungu) 
adzakhala (Akusangalala) 
m'minda ndi Mu akasupe 
okongola, 

16. Uku akulandira zimene 
wawapatsa Mbuye wawo (malipiro 
aulemu); Ndithu, iwo amachita 
zabwino Asanapeze izi. 

17. Nthawi yausiku amagona 
pang'ono, (Amadzuka nachita 
mapemphero Mochulukitsa), 

18. Ndipo kum'bandakucha, 
iwo Amapempha chikhululuko, 

19. Ndipo m'chuma Chawo 
mudali gawo (Lodziwika) la 
opempha Ndi osapempha (mwa 
osauka). 



20. M'nthaka muli zizindikiro 
kwa Otsimikiza, (Zosonyeza kuti 
Mulungu alipo). 



£$ay£a*g# 



yiMS3f-'>*< 



®v&Mfr$i. 



SOj 






*&&&$&&& 









<e SB*SV - w11 '" 



& 



Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 26 1 129 n * >» * i ob iJUi 5^ 



21. Ndi mwa inu nomwe; Kodi 
simuona? 

22. Ndipo kumwamba kuli 
Zokuthandizani (pa moyo wanu), 
ndi Zimene mukulonjezedwa. 

23. Ndikulumbirira Mbuye wa 
kumwamba Ndi pansi, 
ndithu,zimenezo ndi zoona 
Monga kulili Kuyankhula kwanu. 

24. Kodi yakufika nkhani ya 
alendo a Ibrahim; (angelo) 
Olemekezeka? 

25. Pamene adalowa kwa iye 
ndi Kunenakuti: "Salaam", 
("Mtendere")! Iye 
Adayankha:"Salaam" ("Mtendere) 
inu Ndinu anthu osadziwika 
(achilendo)". 

26. Adatembenukira kwa 
akunyumba ake 

(Mwakachetechete), ndipo adadza 
Ndi nyama ya mwana wa ng'ombe 
Yonona (yowotcha). 

27. Naipereka kwa iwo (koma 
sadadye); Iye adanena (modabwa): 
"Kodi bwanji Simukudya?" 

28. Mumtima mwake 
adadzazidwa manthaNdi iwo. Iwo 
adati: "Usaope," Ndipo adamuuza 
nkhani yabwino Ya kubala mwana 
wodziwa. 

29. Adadza mkazi wake ndi 
mkuwe (Pamene adamva nkhani 









&,,& 



i*M*fc$to& 






Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 27 1 130 TV * j*-i \ oUjiJUi 5 ^ 



yabwino ija). Adadzimenya 
kunkhope (ndi dzanja lake 
Kusonyeza kudabwa ndi 
kusatheka). Ndipo Adati: ("Ine 
ndine) nkhalamba (Ndiponso) 
chumba; (ndingabereke Bwanji)?" 

30. Iwo adati: "Momwemo, 
Mbuye wako wanena. lye 
Ngwanzeru Zakuya (pa 
chilichonse chimene Akulamula); 
Ngodziwa; (palibe Chimene 
chingabisike kwa lye). 

31. (Ibrahim) adati: "Kodi 
mwadzanso Nchiyani? E, inu 
otumidwa!" 

32. Iwo adati: "Tatumizidwa 
kwa Anthu oipa . 

33. Kuti tiwagende ndi miyala 
Yotenthedwa Kuchokera kudongo. 

34. Yoikidwa chizindikiro cha 
Aliyense wochimwa kuchokera 
kwa Mbuye wako." 

35. Okhulupirira omwe adali 
m'mudzimo, tidalamula kuti 
atuluke. 

36. Sitidapeze mmenemo 
(okhulupirira Ambiri) kupatula 
mnyumba imodzi Ya Asilamu. 

37. Ndipo tidasiya pamenepo 
Chizindikiro (chosonyeza 
kuonongeka kwa eni mudziwo kuti 
chikhale lingaliro) Kwa amene 
akuopa chilango Chopweteka. 






^\^4ysv^ 



© 









Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 27 1 1131 I TVt>i \ oUjiJUi 9JJ * 



38. M'nkhani ya Musa (muli 
phunziro) Pamene tidamtuma kwa 
Farawo uku Atalimbikitsidwa ndi 
chisonyezo Choonekera. 

39. Koma Farawo adanyoza 
(kukhulupirira Musa) chifukwa 
chotama nyonga zake, Ndipo adati: 
"Uyu ndi wamatsenga kapena 
Wamisala". 

40. Tidamlanga pamodzi ndi 
khamu lake La nkhondo ndi 
kuwaponya mnyanja; iye ali 
Wodzudzulidwa. 

41. Ndipo m'nkhani ya Adi 
(muli phunziro) Pamene 
tidawatumizira chimphepo 
(Chamkuntho) chopanda chabwino 
mkati Mwake. 

42. Chomwe sichisiya chinthu 
chimene Chachidutsa koma 
kuchichita monga Chofumbwa. 

43. Ndipo m'nkhani ya Samudu 
(Muli chisonyezo) pamene 
Kudanenedwa kwa iwo kuti: 
"Sangalalani (mnyumba zanu) 
mpaka Nthawi yakutiyakuti." 

44. Koma adadzikweza 
(ponyozera) Lamulo la Mbuye 
wawo. Choncho Chiphokoso 
chidawaononga uku Akupenya. 

45. Sadathe kuimirira ndi 
(kuthawa) Ndiponso sadali 
Wodzipulumutsa. 



9 & 



^»a5A»i^J3 









^i^^f^A^^^h $*$> 



k^i&&\\p&&z. 



L 9 ™* 






J*X 1 \\9 9 J* <"$< 9 *' 9\ 9'x9? 






%&$&^jx®& 



Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 27 1 \ 132 | Y V » j*-i 1 obji JUi Sjj- 



46. Naonso anthu a Nuhi 
(Tidawaononga) kale chifukwa 
iwo Adali anthu otuluka 
mchilamulo (cha Mulungu). 

47. Thambo tidalimanga 
mwamphamvu (ndi Luntha); ndipo 
tingathe kuchita zochuluka 
(Kuposa zimenezi.) 

48. Ndipo nthaka tidaiyala; 
Taonani kukonza bwino Ife amene 
tidakonza nthaka! 

49. Chinthu chilichonse 
tachilenga Ziwiriziwiri kuti inu 
mulingalire (Ndi kukhulupirira 
mphamvu Zathu). 

50. Thawirani kwa Mulungu. 
Ine ndine Mchenjezi woonekera 
kwa inu Wochokera kwa lye. 

51. Ndipo musadzipangire 
Mulungu wina Wompembedza ndi 
kumuphatikiza ndi Mulungu. Ndithu, 
ine ndine mchenjezi Woonekera 
poyera kwa inu wochokera Kwa lye. 

52. Momwemo (ndimo idalili 
mibadwo Yakale pamodzi ndi 
aneneri awo); Palibe Mthenga 
amene adawadzera Anthu akale, 
anthu akowa kulibe, Popanda 
kumnena kuti: "Ndiwamatsenga 
kapena wamisala." 

53. Kodi adalangizana za 
mawuwa Pakati pawo? Iyayi, 
koma iwo Ndianthu opyola Malire. 






®<&2$§3 ^*^yi4A^-^5 









f %P&X$i&& 



Surat 51. Adh-Dhariyat Juzu 27 1133 TV *>i o ^ ob>iJUi 0^ 



54. Choncho apatukire iwo 
(amakani.) I we suli 
wodzudzulidwa (pakuleka Kwawo 
kuyankha kuitana). 

55. Kumbutsa. Ndithu, 
Kukumbutsa kumawathandiza 
Okhulupirira. 

56. Sindidalenge ziwanda 
(majini) ndi Anthu koma kuti 
Azindipembedza. 

57. Sindifuna kwa iwo 
chithandizo Ndiponso sindifuna 
Kuti azindidyetsa. 

58. Ndithu Mulungu ndi Amene 
ali ndi udindo wopatsa anthu Ake 
madalitso; lye ndi Mwini 
mphamvu Zoposa; Wolimba, 
(salaphera kanthu). 

59. Ndithu, amene adzichitira 
okha Chinyengo (pokana ndi 
kutsutsa) Ali nalo gawo la 
chilango monga Gawo la anzawo 
(a mibadwo yakale); Choncho 
asandifulumizitse (kutsitsa 
Chilango nthawi yake isanafike)! 

60. Kuonongeka kuli pa amene 
atsutsa za Tsiku lawo limene 
alonjezedwa. 



y«sBj**E5 



^fe»«^3MSJ6 



*&^C!&$£®z 



9f \gl 



©SfJiiftldl&tf^s 






fi 9& 9 \99<$ '9 m #*(9l9'< 




Surat 52. At-Tiir Juzu 27 



1134 



rv*>i 



oy jjiaJ' ^J*** 




SURAT AT-TUR LII 




Surayi yayamba ndikulumbirira zinthu zisanu mwa 
zolengedwa zikuluzikulu potsimikiza kuti chilango chiwapeza 
otsutsa, ndi kufotokoza m'mene chidzawapezere pamodzinso 
ndi mitundu yake, pa tsiku la chiweruzo ndi kuuka ku imfa. 
Yafotokozanso za nkhani ya mtendere kwa oopa Mulungu ndi 
zimene azikasangalala nazo mu minda yamtendere yamuyaya, 
kudzanso mitundumitundu yaulemu umene azikalandira 
kumeneko. Ndipo akawasangalatsanso powakumanitsa ndi ana 
awo amene zochita zawo zabwino zidali zochepera poyerekeza 
ndi zamakolowo. 

Surayi yapitiriza ndi kulamula Mneneri (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) kuti awasiye mpaka adzakumane ndi 
tsiku limene adzaonongedwa. Ndipo yamulamula kuti apirire 
ndi lamulo la Mbuye wake lolekerera osakhulupirirawo 
osawalanga msanga, ndi kuti pazimenezi palibe vuto limene 
lingampeze lye akumyang'anira ndi kumsunga. Ndipo 
wauzidwanso kuti apitirize kulemekeza Chauta ndi kumpatula 
ku makhalidwe osayenerana ndi makhalidwe ake, makamaka 
nthawi yolowa nyenyezi. 




Surat 52. At-Tiir Juzu 27 1135 rv»>i 



1 jjlaJl i jj»- 



Surat At-Tur LII 



a ^ -?■-*■ ''" 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira phiri la Turi 
(ku Sinai Pamene Musa 
adalankhulana Ndi Mulungu). 

2. Ndi Buku lolembedwa. 

3. M'mipukutu yazikopa 
zotambasuka (Zosavuta kuwerenga); 

4. Ndi nyumba yopitako 
kawirikawiri (Pochitamo 
mapemphero). 

5. Ndi thambo limene 
latukulidwa (Popanda mzati); 

6. Ndi nyanja yodzadza ndi 
madzi. 

7. Ndithu, chilango cha Mbuye 
wako (Chimene wawalonjeza 
nacho Osakhulupirira) chiwapeza 
(Popanda chipeneko); 

8. Palibe wochichotsa (pa iwo). 

9. Pa tsikulo thambo 
lidzagwedezeka; Kugwedezeka 
kwamphamvu. 

10. Ndipo mapiri adzachoka 
m'malo Mwake (moonekera). 

11. Kuonongeka koopsa pa 
tsiku Limenelo kuzakhala pa 
Otsutsa choonadi; 



o^l^l^W- 



— w 



v # i& 



QJM 



Z0i$A 



™ ^ - %4*& 



t'li *1Li\ 



*>"\\ 9'\\' 






%^&< 
HP&&A 






Surat 52. At-Tur Juzu 27 



1136 tV*>i 



Y J^^' ^Jj^ 



12. Iwo amene akungosewera 
Mzinthu zopanda pake. 

13. Tsiku limene 
adzakankhidwira Mwamphamvu 
ku Jahannama (kumoto Woopsa). 

14. (Kudzanenedwa kwa iwo): 
"Uwu ndi Moto uja umene mudali 
kuutsutsa (Padziko lapansi) 

15. Kodi awa ndi matsenga 
Kapena inu simukuona? 

16. Lowanimo, (mulawe 
kupsereza Kwake) pirirani (ndi 
mavuto ake) Kapena musapirire, 
ndichimodzimodzi Kwa inu. Ndithu 
mulipidwa pazimene Munkachita." 

17. Ndithu oopa Mulungu 
adzakhala M'minda yamtendere 
(yotambasuka Yosasimbika 
kukongola kwake) Ndi 
chisangalalo chachikulu. 

18. Uku akukondwerera zimene 
wawapatsa Mbuye wawo ndi 
kuwatchinjiriza ku Chilango 
chamoto. 

19. (Kudzanenedwa kwa iwo): 
"Idyani (Chakudya chamtendere); 
ndipo imwani Mosangalala 
kukhala malipiro pazimene 
Munkachita padziko lapansi. 

20. Uku atakhala moyadzamira 
pa Mipando yondandika bwino ndi 
Kuyalidwa bwino; ndipo 
Tidzawakwatitsa akazi Ophanuka 
maso mokongola. 



%#&*&#&* 



^ZfZ^j&ft* S 



®cfi^S?$»&$» 



ojj^^bliuJ^^l 






9>K 






^$^&$$ 



*V.'''.'Va'-*1 *» >> 'li " (** 



Surat 52. At-Tur Juzu 27 



1137 



YV*j*-i 



OX jjlaJl ^JJ -- 



21. Ndipo amene akhulupirira 
Ndipo ana awo nkuwatsatira Pa 
chikhulupiriro tidzawakumanitsa 
iwo Ndi ana awowo ndipo 
sitikawachepetsera Kalikonse 
m'mphoto za ntchito zawo; 
Munthu aliyense adzakoledwa ndi 
Zochita zake; 

22. Ndipo tidzawaonjezera 
Zipatso ndi nyama imene 
Adzakhala akuilakalaka. 

23. Azikalandirana m'menemo 
(Mwachikondi wina ndi mnzake) 
chikho Chodzazidwa ndi 
zakumwa; Sipakakhala kwa iwo 
zolankhula Zachabe ngakhale 
zochita zamachimo. 

24. Ndipo azikawazungulira 
anyamata Owatumikira onga ngale 
yosungidwa M'chigoba chake 
(kukongola kwawo) 

25. Azidzatembenukirana wina 
ndi Mnzake uku akufunsana (za 
kukula Kwa mtendere umene 
adzakhala Nawo ndi kuti adaupeza 
chotani). 

26. Adzanena: "Ife tidali oopa 
chilango Cha Mulungu pakati pa 
maanja athu (Tisadalandire 
mtendere wu). 

27. Ndipo Mulungu watidalitsa 
ndipo Watitchinjiriza ku chilango 
chamoto: 



(99 ' 






"&£%'fi'$hl&d$£ 



©, 



,MVA 






*& 



®Q^%3&M$ 



©yj^cJ&LSjij^&IgS 



Surat 52. At-Tur Juzu 27 



1138 



rv $.>i 



y j^q}\ Ojj-*» 



28. Ndithu, ife timampembedza 
(Kalero padziko lapansi) ndithu 
lye Yekha ndiye wabwino 
Ngwachifundo." 

29. Choncho, kumbutsa,iwe suli 
mlosi Kapena wamisala 
pamtendere wa Mbuye wako; 

30. Kapena akukunena iwe kuti 
ndiwe Mlakatuli, 
tikumuyembekezera, Imfa impeze. 

31. Nena (kwa iwo moopseza) 
"Yembekezerani! Ndithu ine ndili 
nanu Mwa mmodzi 
woyembekezera." 

32. Kapena nzeru zawo ndizo 
Zikuwauza izi kapena iwo Ndi 
anthu opyola malire. 

33. Kodi akunena kuti: 
"Wadzipekera 

(Mtumiki{SAW}Qur'an)"? Iyayi, 
koma Iwo sakukhulupirira. 

34. Atabwera ndi nkhani 
yofanana ndi iyo (Qur'an) ngati ali 
oona m'kuyankhula Kwawo (koti 
Mtumiki{SAW}wapeka Qur'an.) 

35. Kapena adalengedwa 
popanda Mlengi Kapena iwo 
adadzilenga okha (Nchifukwa 
sakuvomereza za Mlengi 
Wopembedzedwayo?) 

36. Kodi ndiwo adalenga thambo 
Ndi nthaka? Koma satsimikiza 
(Zoyenera kumchitira Mlengi) 















Surat 52. At-Tur Juzu 27 



1139 



YV t>l 



O Y jjiaJl 5j>w 



37. Kodi nkhokwe (za zabwino) 
za Mbuye wako zili ndi iwo 
(kotero Kuti akuzigwiritsa ntchito 
mmene Angafunire?) Kapena iwo 
Ngopambana? 

38. Nanga kodi ali nawo 
makwerero (Amene akukwerera 
kumwamba) Kotero kuti 
akumvetsera zimene Mulungu 
akulamula? Choncho, omvetsera 
Awo abwere nawo umboni 
owonekera (Osonyeza kuona 
kwawo Pazimene akunenazi). 

39. Kodi lye (Mulungu) ndiye 
Ali ndi ana akazi ndipo inu muli 
ndi ana Aamuna? 

40. Kodi ukuwapempha malipiro 
Alionse (pofikitsa uthenga); 
Kotero kuti iwo akulemedwa ndi 
Kulipira (uthengawu)? 

41. Kodi iwo amadziwa zamseri 
kotero Kuti iwo akumalemba 
(Zimene afuna)? 

42. Kapena akufuna kukuchitira 
chiwembu (Ndikuononga uthenga 
wako?) Koma Amene 
sadakhulupirire ndiwo omwe 
Chiwabwerere chiwembu (chawo.) 

43. Kodi ali naye 
wompembedza, osati Mulungu 
(amene angawateteze ku Chilango 
cha Mulungu)? Mulungu 
Wapatukana ndi zimene 
akumuphatikiza Nazo. 






^Ij&'^&f 



4^&&»&a&p 



Hs&&$$&& 






%W£^wmi)& 



Surat 52. At-Tur Juzu 27 



1140 



YV tjJt-i 



Ot jjkil 5jj-*> 



44. Koma akaona gawo 
lathambo Likugwa (kuti liwalange) 
akunena (Mwamakani ndi 
kunyada): "Uwu ndi Mtambo 
umene wasonkhanitsa Madzi a 
mvula." 

45. Asiye; (usalabadire za iwo) 
mpaka Pomwe adzakumana ndi 
tsiku lawo Limene 
adzaonongedwa, 

46. Tsiku lomwe chiwembu 
chawo Sichidzawathandiza 
chilichonse; Ndipo iwo 
sadzapulumutsidwa. 

47. Ndipo ndithu, amene achita 
Zosalungama ali nacho chilango; 
Chosakhala chimenecho (chilango 
Chimene akuonongedwa Nacho 
padziko lapansi)! Koma Ambiri a 
iwo sadziwa (zimenezi). 

48. Ndipo pirira ndi lamulo la 
Mbuye wako Ndithu, iwe ndiwe 
wosungidwa ndi Kuyang'aniridwa 
ndi Ife; ndipo Lemekeza ndi 
kumyamika Mbuye Wako pamene 
ukuimirira, 

49. Ndipo m'gawo la usiku 
Mlemekeze lye ndi nthawi yolowa 
Nyenyezi'. 


















hf^O^^^*^ ££ 



Surat 53. An-Najm Juzu 27 I 1141 1 TV *£?\ or p*Jt Sjj-* 




Kulumbira koyambirira kwa Surayi kukuonetsa poyera kwa 
Mneneri (madalitso ndi mtendere zikhale naye) pazimene 
akufotokoza m'nkhani ya chivumbulutso ndi uthenga umene 
akulalikira wa chivumbulutsocho. Sadasokere ndi 
chivumbulutsocho ndipo sadalakwe chilichonse, koma akunena 
zoona pazimene akufotokoza paulendo wake wonka kumwamba 
m'nkhani (ya Miraj). Maso ake sadasokonezeke pazomwe 
adaziona ndipo sadapyole malire. 

Kenako Surayi ikulongosola nkhani ya kufooka kwanzeru za 
osakhulupirira namapembedza mafano omwe adadzipangira ndi 
manja awo ndi kuwatcha okha maina, monga momwe adatchera 
angelo kuti ndi akazi, ndi kutinso ndi ana aakazi a Chauta, 
pomwe iwo adadzisankhira ana aamuna. 

Ndipo popitirira Surayi ikulangiza Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) kuti apatukane nawo ndi kumusiyira 
Mulungu zochita zawo, Amene ndi Mwini kumwamba ndi 
pansi; Mwini kulenga. Ndiponso ndi Amene adzalipira wochita 
zoipa, zoipa zake; wochita zabwino, zabwino zake. lye 
Ngodziwa kwambiri kusinthasintha kwa chilengedwe cha 
munthu ndi chikhalidwe chake. Ndipo akuchenjeza amene 
akukana kuweruzidwa ndi munthu aliyense pa zochita zake 
monga momwe zidalongosolera zipembedzo zakale. Ndipo 
kalata za Musa ndi Ibrahim zidafotokozanso zomwezo. 

Surayi yamaliza ndi kunenetsa kuti Qur'an ndi mchenjezi 
monga mo we adalili achenjezi akale amene adachenjeza 
mibadwo yakale kuti iope tsiku lachiweruziro limene nthawi 
yake ili pafupi, ndipo kumapeto kwake yapempha Asilamu kuti 
amulambire Mulungu. 



Surat 53. An-Najm Juzu 27 1142 TV *>i 



Of *J!tJl Ijy* 



Surat An-Najm LIII 



n* v> 



*:":;; mm 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbira nyenyezi 
pamene Zikulowa. 

2. Sadasokere m'bale wanu 
(Mtumiki Panjira ya choonadi) 
ndipo sadakhulupirire Zonama. 

3. Ndipo sayankhula zofuna za 
mtima wake. 

4. Iyoyi (Qur'an imene 
akuinena), sichina, Koma 
ndichivumbulutso 
Chovumbulutsidwa. 

5. Adamphunzitsa 
(chivumbulutsochi) (Jibril) 
wanyonga zambiri, 

6. Wanzeru zakuya; ndipo 
adakhadzikika (M'maonekedwe 
ake). 

7. Ali m'chizimezime 
kumwamba. 

8. Kenako (Jibril) 
adamuyandikira (Mtumiki {SAW}) 
ndikuonjezera Kumuyandikira, 

9. (Kumuyandikira kwake) 
kudali ngati (Mpata wa) nsonga 
ziwiri za uta, kapena Kuyandikira 
kuposa apo; 



ofa$\<&$\&\j 






Surat 53. An-Najm Juzu 27 1143 TV ^jJt-i 



Or p*dl 5jj~> 



10. (Choncho Jibril) 
adavumbulutsira Kapolo Wake 
(wa Mulungu) zimene 
Adazivumbulutsa. 

11. Sudaname mtima (wa 
Mtumiki) Pazimene adaziona. 

12. Kodi mukutsutsana naye 
(Mthenga wa Mulungu) pazimene 
adaziona 

13. Ndipo ndithu, adamuona 
(Jibril) M'kuona kachiwiri 
mkaonekedwe kake. 

14. Pa 'Sidiratil Muntaha' 
(mtengo Wamasawu pothera 
zinthu zonse). 

15. Pafupi pake pali Janatu 
Ma'awa, (munda wokhalamo) 

16. Pomwe chophimba 
chidaphimba Msawuwo. 

17. Maso ake sadaphonye 
Kapena kupyola malire (oikidwa) 

18. Ndithu, (Mneneri 
Muhammad{SAW}) adaona zina 
mwa Zizindikiro zikuluzikulu za 
Mbuye wake (Zosonyeza 
mphamvu Zake) 

19. Kodi mwawaona Lata ndi 
Uzza. 

20. Ndi Manata; fano (lanu) lina 
Lachitatu, (kuti iwowa ndi 
milungu)? 






© j^C'jj^^X' 



^^t*#oaJ 



&$&&%$ 



©o^^ys 



Surat 53. An-Najm Juzu 27 



1144 



YVfrjA-i 



Of a^cJl ^J-** 



21. Kodi mwadzisankhira ana 
Achimuna (kukhala anu), ndi 
achikazi Nkukhala a lye (Mulungu)? 

22. Choncho kugawa kumeneko 
nkopanda Chilungamo (pompatsa 
Mulungu zimene Mumazida). 

23. Sali (mafanowo) 
chilichonse koma ndi Maina basi 
omwe mudawatcha inu ndi Makolo 
anu, (molingana ndi zilakolako 
zanu zachabe); Mulungu sadatsitse 
Umboni pazimenezo (wotsimikiza 
Pamawu anuwo). Sakutsatira koma 
Zoganizira basi ndi zimene 
Ikufuna mitima (yawo yopotoka). 
Ndithu, chidawadzera chiongoko 
Kuchokera kwa Mbuye wawo 
(chomwe M'kati mwake mudali 
kuongoka Kwawo akadachitsatira). 

24. Kodi munthu akuganiza kuti 
Adzapeza chilichonse chimene 
Akuchilakalaka? 

25. Tsiku lomaliza Ndi dziko 
lapansi nza Mulungu yekha. 

26. Ndipo kuli Angelo ambiri 
kumwamba Omwe kuchonderera 
kwawo sikungathandize China 
chilichonse pokhapokha Mulungu 
Ataloleza kwa amene Wamfuna 
ndi kumuyanja 

27. Ndithu, amene sakhulupirira 
za (Moyo wa) tsiku lomaliza, 
amatcha Angelo kuti ndiakazi; 









Surat 53. An-Najm Juzu 27 



1145 



rv ftj*-i 



OT ^cJl 5jj-j 



28. Ndipo alibe kudziwa 
kulikonse pa zimenezo Sakutsata 
china koma maganizo ndithu, 
Kuganizira sikuthandiza 
chilichonse Pofuna kupeza 
choonadi. 

29. Choncho apewe 
(osakhulupirirawa) Amene 
anyozera Qur'an Yathu; ndipo 
palibe Chimene akufuna koma 
Umoyo wa padziko lapansi basi. 

30. Zimenezo ndiwo mapeto A 
kudziwa kwawo. Ndithu, Mbuye 
Wako Ngodziwa kwambiri za 
amene Akusokera njira Yake 
Ndiponso akudziwa bwino za 
yemwe Wawongoka. 

31. Ndipo zonse za kumwamba 
ndi zadziko Lapansi nza Mulungu 
Yekha, (Pozilenga ndi 
kuziyang'anira), Kuti adzawalipire 
amene adaipitsa pazimene 
Adachita ndi kutinso adzawalipire 
zabwino Amene adachita zabwino. 

32. Amene akuwapewa 
machimo Akuluakulu ndi zadama, 
kupatula Timachimo 
tating'onoting'ono (timene 
Mulungu amatikhululuka); ndithu, 
Mbuye wako ndiwokhululuka 
Kwakukulu.Iye akudziwa 
chikhalidwe Chanu kuyambira 
pomwe adakulengani Kuchokera 
m'nthaka ndi pamene inu Mudali 






©(JOCftl 









Surat 53. An-Najm Juzu 27 I 1146 1 *V *j*-' 



or j^idi-Sjj-. 



makanda m'mimba mwa amayi 
Anu (mosinthasintha; 
mosiyanasiyana). Choncho 
musadzitame nokha kuyera 
Mtima; lye adziwa kwambiri za 
yemwe Akuopa (Mulungu). 

33. Kodi wamuona yemwe 
wadzipatula (Pakusiya kutsatira 
choonadi)? 

34. Ndipo wapereka (chuma) 
chochepa Nasiyanso kuperekako. 

35. Kodi akudziwa zamseri, 
kotero kuti Akuziwona (zomwe 
wadza nazo (Mtumiki{SAW} kuti 
sizoona)? 

36. Kapena sadauzidwe zomwe 
zidali M'mabuku a Musa, 

37. Ndi Ibrahim amene 
adakwaniritsa (Lonjezo la 
Mulungu)? 

38. Kuti mzimu wamachimo 
sungasenze Machimo a mzimu wina 

39. Ndi kutinso munthu 
sakalipidwa Koma zimene adachita; 

40. Ndipo ndithu, ntchito Zake 
zidzaonekera. 

41. Kenako (munthu) 
adzalipidwa malipiro Okwanira 
(pantchito zake zimene Amachita). 

42. Ndipo ndithu, kwa Mbuye 
wako yekha Ndiwo malekezero (a 
chilichonse) 



9 .ft '9*SC\ 



V T '9. *Zi'9 \9\' 






$mm& 



^BSft&JjfiS 



Surat 53. An-Najm Juzu 27 I 1147 tv ^j*-i 



of *^«Ji ^j>^ 



43. Ndithu, lye ndiAmene 
amapereka Chisangalalo ndi 
zoliritsa; 

44. Ndipo lye yekha ndiAmene 
Amapereka imfa ndi moyo. 

45. Ndipo lye ndiAmene 
adalenga mitundu Iwiri: 
chachimuna ndi chachikazi, 
(Anthu ndi zamoyo zina). 

46. Kuchokera m'mbewu ya 
moyo pamene Imafwamphukira 
(m'chiberekero). 

47. Ndipo ndithu, ndi udindo 
Wake kuukitsa Kwina (pambuyo 
pa imfa). 

48. Ndipo lye ndiAmene 
amapatsa Chokwanira ndipo ndi 
Amene Amapatsa chosunga; 

49. Ndipo ndithu, lye ndi 
Mbuye Wa Nyenyezi Iyo 
yotchedwa Shiira; 

50. Ndipo lye ndi Amene 
adaononga Adi oyamba; (anthu a 
Mneneri Hud). 

51. Ndi Samudu; (anthu a 
Mneneri Swaleh; )sadasiye (ndi 
mmodzi Yemwe wa iwo). 

52. Ndipo (adawaononganso) 
anthu a Nuhi, Kale (asadaononge 
Adi ndi Samudu). Ndithu iwo adali 
osalungama Ndi olumpha malire 
Kwambiri (kuposa Adi ndi Samudu). 



ft &1Rf^3j 






Surat 53. An-Najm Juzu 27 I n48 I *V *j*-i 



df *^cJl 5jj-j 



53. Ndi midzi 
yotembenudzidwa Kumwamba 
kukhala Pansi, pansi kumwamba, 
(Ya anthu a Luti), adaigwetsa. 

54. Chidaivindikira chomwe 
Chidaivindikira (Chilango). 

55. Kodi ndimtendere uti 
(Mumtendere) wa Mbuye Wako 
umene ukuukaikira? 

56. Uyu (Mtumiki) 
ndimchenjezi mwa Achenjezi 
oyamba (amene adachenjezedwa 
Nawo anthu a mibadwo yakale) 

57. Tsiku lachiweruzo 
layandikira. 

58. Palibe angaonetse koma 
Mulungu yekha. 

59. Kodi mukuidabwa nkhaniyi 
(Ya Qur'an moikana)? 

60. Mungoseka 
(mwachipongwe) ndipo 
Simukulira (pamene mukuimva 
monga Momwe akuchitira 
okhulupirira), 

61. Ndipo mukunyozera? 

62. Mlambireni ndi 
kumpembedza Mulungu (Amene 
wavumbulutsa Qur'an Kuti ikhale 
chiongoko cha anthu). 



§&mm 






e03Su55M£^^ 












Surat 54. AI-Qamar Juzu 27 I 1149 I TV *jJM 1 j+&\ oj>- 




SURAT AL-QAMAR LIV 




Ndime yoyamba m'sura iyi ikufotokoza zakuyandikira kwa 
tsiku lachiweruzo ndi kuwachenjeza anthu za chiweruzocho. 
Pambuyo pake padza ndime zofotokoza maganizo a osakhulupirira 
zozizwitsa za Mulungu ndi kupitiriza kusakhulupirira kwawo. 

Ndipo Surayi ikupempha Mtumiki (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye), kuti awapewe osakhulupirira ndi kuwalekerera 
mpaka kufikira tsiku lotuluka m'manda pomwe adzakhale 
balalabalala ngati dzombe. Pambuyo pa zimenezi Surayi 
yalongosola mbali ya chikhalidwe cha mibadwo yakale pamodzi 
ndi aneneri awo ndi chilango chomwe chidawapeza. Ndipo 
yafotokoza nkhani ya aliyense wa iwo ndi kutsimikiza kuti 
Qur'an ndi yofewa kwa munthu amene akufuna kuilingalira. 

Surayi yamaliza ndi kulongosola kuti osakhulupirira a m' 
Makka sianyonga ngati mibadwo imene idatsogola, ndi kuti iwo 
alibe mtendere ku chilango cha Mulungu. Ndipo kumapeto 
kwenikweni Surayi yaopseza otsutsa, za mabwerero awo pa 
tsiku limene adzakokedwe nkhope zawo ndi kuponyedwa ku 
moto. Kudzanenedwa kwa iwo panthawiyo: "Lawani 
kupweteka kwa Jahena imene mumaitsutsa!" 

Ndipo oopa Chauta akuwatonthoza powauza kuti adzapita 
kumalo awo m'minda ndi m'mitsinje yambiri pokhala pabwino 
kwa Mfumu ya mphamvu zoposa. 




Surat 54. Al-Qamar Juzu 27 1150 TV *j*-i 



o t j^iil ijj^t 



Surat Al-Qamar LIV 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nthawi ya chimaliziro 
(Kiyama) Yayandikira ndipo 
Mwezi wagawikana. 

2. Koma akaona chozizwitsa 
akunyoza Ndi kunena kuti: "Awa 
ndi matsenga Womkeramkera 
patsogolo." 

3. Ndipo adatsutsa (choonadi) 
ndi kutsatira Zilakolako (zawo 
zoipa) koma Chinthu chilichonse 
(cha Mulungu) Nchokhazikika. 

4. Ndipo ndithu, zidawafika 
nkhani Zomwe zili zokwanira 
Kuwaopseza. 

5. Nzeru zokwana koma 
Achenjezi (kwa iwo) 
Sanawathandize. 

6. Choncho, apewe (iwe 
Mtumiki) Osakhulupiria, 
(yembekezani) tsiku Loitana 
woitana (wa Mulungu) Kuchinthu 
chovuta kwambiri, (Chodedwa ndi 
mitima). 

7. Maso awo ali zyoli chifukwa 
Chakuopsa; adzatuluka m'manda 
Uku ali ngati dzombe lobalalika 
(Chifukwa cha kuchuluka), 









oj&&\(&*-3\£Aj 



'J> 



®p\&\;%m<£Mi 






£&r£'&mm> 



© 



i-''i 



^&M&£&& 



®^\&s$& 



ig&m^g&zz 






Siirat 54. Al-Qamar Juzu 27 I 1151 I TV *>' 



O t j^ill d jj-> 



8. Akuthamangira kwa woitana 
(uku Atatukula mitu yawo, osatha 
Kucheukira kwina).Adzanena 
Osakhulupirira (tsiku 
lachiweruziro): "Hi nditsiku lovuta 
kwambiri." 

9. Patsogolo pawo (Aquraishi) 
Anthu a Nuhi nawo adatsutsa, 
Adamtsutsa kapolo Wathu nanena 
kuti: "Uyu ngwamisala!? Ndipo 
Adaopsezedwa (ndi kuzunzidwa 
Ndi mazunzo osiyanasiyana). 

10. (Nuhi) adaitana Mbuye 
wake (nati): "Ine ndagonjetsedwa 
(ndi anthu anga); Choncho 
ndipulumutseni (kwa iwo)." 

11. Tidatsekula makomo 
akumwamba Ndi madzi otsika 
mopitiriza, Mwamphamvu. 

12. Ndipo tidaing'amba nthaka 
kukhala ndi Akasupe ofwamphuka 
madzi Mwamphamvu. Choncho 
adakumana Madzi (akumwamba 
ndi am' nthaka Kuti awaononge) 
pamuyeso Wopimidwa ndi 
kulamulidwa (Ndi Mulungu). 

13. Ndipo tidanyamula Nuhu pa 
chombo Chamatabwa 
chokhomedwa ndi Misomali 
(yamitengo) 

14. Chinkayandama pamadzi 
ndi Kuyang'aniridwa ndi Ife. Iyi 
ndi Mphoto ya (Nuhi) yemwe 
adakanidwa Ndi anthu ake. 



ioifc3»ffig^aa^ 









<^#s3jP8fcui 






^iMdtf&s 



®$3&*4W 



Surat 54. Al-Qamar Juzu 27 I 1152 * V *>i 



£ yjti\ 5jj-*» 



15. Ndipo ndithu, tidachisiya 
(chigumula) Kukhala phunziro 
(pakuonongeka kwa 
Osakhulupirira ndi kupulumuka 
Okhulupirira).Kodi alipo 
Wolikumbukira (ndi kupeza nalo 
Malango abwino?) 

16. Kodi chidali bwanji 
chilango Changa ndi machenjezo 
Anga (Kwa onyoza!) 

17. Ndipo ndithu, taifewetsa 
Qur'an kuti Ikhale chikumbutso 
kodi alipo Woikumbukira (ndi 
kupeza nayo Malango abwino?) 

18. (Adi adamtsutsa Mneneri 
wawo Hudi), Kodi chidali bwanji 
chilango Changa ndi machenjezo 
anga Kwa onyoza! 

19. Ndithu Ife tidawatumizira 
mphepo Yozizira, yaphokoso, 
m'tsiku Latsoka lopitirira, 

20. Idawazula anthu (kuchoka 
m'malo Mwawo ndi kuwaponya 
panthaka Ali akufa) ngati matsinde 
a Mitengo yakanjedza ozulidwa 
M'malo mwake. 

21. Kodi chidali bwanji 
chilango Changa ndi machenjezo 
anga kwa Onyoza! 

22. Ndithu, taifotokoza Qur'an 
kuti ikhale Chikumbutso. Kodi 
alipo Woikumbukira (ndi kupeza 
nayo Malango abwino?) 



®1®&&W3& 



®&b&&£& 



®p$&&M^A&> 



©, 



^3i)\&$<3i&% &wd? 



®gSX 






'S&3M ^ ffi ^-^ ^& 



<3> 






Surat 54. AI-Qamar Juzu 27 



1153 



tV*>i 



t j^iil Oj_^-* 



23. Asamudu adatsutsa achenjezi. 

24. Ndipo adati: "Kodi titsatire 
munthu Mmodzi wochokera mwa 
ife? Ndithu Ife ngati titamtsatira 
ndiye kuti Tili nkusokera ndiponso 
misala. 

25. Kodi am'vumbulutsira iye 
Chikumbutso pakati pathu, 
(Pomwe tili nawo oposa iye Pa 
ulemerero)? Koma iye 
Ndiwabodza ndi wodzitukumula" 

26. Mawa lino adzadziwa (tsiku 
Lakuwatsikira chilango,) kuti 
ndiyani Wabodza wodzitukumula 
(iwo kapena Swaleh). 

27. (Tidamuuza Mneneriyo 
kuti) ndithu Ife titumiza ngamira 
yaikazi kuti Ikhale mayeso kwa 
iwo. Choncho Adikire, ndipo pirira. 

28. Ndipo auze kuti madzi 
agawidwa Pakati pawo (ndi 
ngamira). Choncho Aliyense ali 
ndi tsiku lopita kukatunga. 

29. Koma adaitana mnzawo (wa 
Mphulupulu). Ndipo adakonzeka 
Kupha ngamirayo ndipo adaipha. 

30. Kodi chidali bwanji 
chilango Changa ndi machenjezo 
Anga (Kwa anthu otsutsa)! 

31. Ndithu, tidawatumizira 
nkuwe Umodzi choncho adakhala 
ngati udzu Ndi mitengo youma 
yaomanga Khola. 






& 



^&gfa&$$$i 



®%\ 



ea^sai a *t&&ȣ. 



J&W 



^^BllA^fy 



* M % 









Surat 54. Al-Qamar Juzu 27 1154 I TV ^jA-i 



1 j^ill 5jj-- 



32. Ndipo ndithu, taifewetsa 
Qur'an kuti Ikhale chikumbutso. 
Kodi alipo Woikumbukira (ndi 
kupeza nayo Malangizo abwino?) 

33. Anthu a Luti adatsutsa 
Machenjezo (a Mneneri wawo). 

34. Ndithujfe tidawatumizira 
chimphepo Champhamvu 
(choulutsa miyala Ndi 
kuwagenda), kupatula akubanja La 
Luti; tidawapulumutsa (ku 
Chilangocho) m'bandakucha, 

35. (Choncho kupulumukako 
kudali) Chisomo chochokera kwa 
Ife (Pa iwo). Momwemo ndimo 
Timamlipirira wothokoza. 

36. Ndipo ndithu (Luti) 
adawachenjeza Anthu ake za kulanga 
Kwathu koopsa. Koma adakaikira 
machenjezo (ake Ndi kumtsutsa). 

37. Ndipo ndithu adafuna kwa 
iye kuti Awapatse alendo ake (kuti 
Achite nawo zauve), koma 
Tidafafaniza maso awo (kuti 
Ikhale mphoto pa zimene 
adafunazo). (Ndipo tidawauza): 
"Lawani Chilango Changa ndi 
machenjezo Anga." 

38. Ndipo chidawadzera 
mwadzidzidzi Chilango 
chokhazikika, nthawi Yam'mamawa. 

39. Choncho (kudanenedwa 
kwa iwo) "Lawani chilango 
Changa ndi Machenjezo Anga." 



^»«j^JS»a*B5S6 






%p>£&®0>&&<& 



i$&ti^®S&8®& 






&2£l££8#£CSS 






Surat 54. Al-Qamar Juzu 27 1155 I TV >>i 



t yj&\ 5jj~»» 



40. Ndipo ndithu, taifewetsa 
Qur'an (Kuti ikhale chikumbutso). 
Kodi alipo Woikumbukira (ndi 
kupeza nayo Malango abwino?) 

41. Ndipo ndithu machenjezo 
(ondondozana) Adawadzera anthu 
a Farawo (ndi iye Mwini;) 

42. Adatsutsa zozizwitsa Zathu 
zonse (Zimene zidadza kupyolera 
m'manja Mwa Aneneri Athu). 
Choncho Tidawaononga, 
kuononga kwa Wamphamvu; 
(Wosapambanidwa). Wokhoza. 

43. Kodi osakhulupirira anuwa 
ndi Abwino kuposa iwo (kotero 
kuti Sadzaonongedwa)? Kapena 
Zalembedwa m'mabuku kuti inu 
Mdzasiyidwa (sadzakuonongani 
monga Momwe adawaonongera 
akale?) 

44. Kapena akunena kuti: "Ife 
Ndiochuluka titha kudziteteza 
(Palibe angatipambane)?" 

45. (Auze): Gululo 
ligonjetsedwa Ndipo athawa ndi 
Kutembenuza misana. 

46. Koma lonjezo la chilango 
chawo ndi Tsiku lachiweruzo, 
ndipo tsiku Lachiweruzo ndi 
latsoka lalikulu, Lowawa kwabasi 
(kwa osakhulupirira). 

47. Ndithu, oipa (mwa awa ndi 
aja) Alinkusokera ndi nchilango 
cha Jahena chopitirira. 



&^j^tyQ\$\%j&& 



k &i 



<& 



$ 












if '.V„9* '>,< ,Atl'*\ 



®Md&?2%& 



@ p\;^\^\^\;^t\a^ 



^X^<5W*3 



Siirat 54. Al-Qamar Juzu 27 11561 *V ^ 



t yjb\ &jy* 



48. Tsiku limene 
adzakokedwera kumoto Ndi 
nkhope zawo, (kudzanenedwa 
Kwa Iwo:) "Lawani zowawa za 
Jahena (Ndi kutentha kwake)! 

49. Ndithu, Ife tachilenga 
chinthu chilichonse Ndi 
muyeso(kulingana ndi Zolinga). 

50. Ndipo silili lamulo Lathu 
(pa chinthu Tikachifuna) koma 
liwu limodzi, (Timangoti kwa 
chinthucho: "Chitika" Ndipo 
chimachitika mwachangu) ngati 
Kuphethira kwa diso. 

51. Ndipo ndithu, tidawaononga 
anzanu (Onga inu osakhulupirira): 
Kodi Alipo okumbuka? 

52. Ndipo chinthu chilichonse 
adachichita Iwowo(padziko 
lapansi) Chili mkaundula. 

53. Ndipo ntchito iliyonse, 
yaing'ono kapena Yaikulu, 
idalembedwa; (palibe Chimene 
chingamsowe). 

54. Ndithu, oopa Mulungu 
adzakhala M'minda ya ulemerero 
waukulu ndi Mitsinje 
(yosiyanasiyana). 

55. Pokhala pabwino 
pachoonadi, (Popanda mawu 
achabe ndi Machimo), kwa Mfumu 
yokhoza Chilichonse. 






*&V&A$&ty 



*j2$tiS^$6*Z 



*&&&j®$®&!& 



®JMP'$& 












Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1157 



TV *>1 



oo Ja^lSj^ 




Surayi ikufotokoza za kuchuluka kwa mtendere wa Mulungu 
umene uli pa anthu. Yayamba ndi kutchula dzina la Mulungu 
loti "Rahman" ndi kutchula mtendere wopambana wonse, 
umene Qur'an ikuphunzitsa. Ndipo kenako yafotokoza za 
mtendere umenewo mwatsatanetsatane kusonyeza ukulu wa 
Mwini mtenderewo, kusonyezanso mphamvu Zake zoposa kwa 
anthu ndi ziwanda kumwamba ndi pansi. Ndipo yasonyezanso 
mmene chidzakhalira chilango cha osakhulupirira Jahena, ndi 
momwe udzakhalira mtendere wa oopa chauta ku mparadiso. 

Surayi yamaliza ndi kupatula Mulungu ku osakhulupirira 
osayenerana ndi lye, komanso kumlemekeza ndi kumtamanda. 




Surat 55. Ar- Rahman Juzu 27 1 158 t V * jJri 



j*J\ Ojj*> 



Surat Ar-Rahman LV 



kfWT^^VTKWX. jZZ-jf— 



S tM$i££ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. (Mulungu) Wachifundo 
Chochuluka! 

2. Waphunzitsa Qur'an. 

3. Adalenga munthu. 

4. Adamphunzitsa kuyankhula. 

5. Dzuwa ndi mwezi zikuyenda 
Mwachiwerengero . 

6. Zomera zopanda tsinde ndi 
mitengo, Zikulambira (Mulungu 
pachilichonse Chimene wafuna 
mwa izo). 

7. Ndipo thambo adalitukula 
kumwamba Ndipo adakhazikitsa 
sikelo (Ya chilungamo), 

8. Kuti musapyole malire ndi 
kuchita Chinyengo poyesa. 

9. Choncho yesani sikelo 
Mwachilungamo Ndipo 
musapungule muyeso. 

10. Ndipo nthaka adaiyala (ndi 
Kuikonza) kuti ikhale ya 
Zolengedwa. 

11. M'menemo muli zipatso ndi 
mitengo Ya kanjedza yokhala ndi 
mapaya (A zipatso). 



^~_^ L^ 



Q^jM^jJl^U- 



-^ 



ty%$ 



"i*t1i.f 



«&2Ji<S£ 






k^ft$&te& 






&JM<&Qmt$K2>, 



Siirat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1159 



rv *>i 



j*J\*jy* 



12. Ndi mbewu zamakoko (kuti 
chikhale Chakudya cha inu ndi 
ziweto zanu), Ndipo mulinso 
m'menemo mmera Wafungo 
labwino. 

13. (Inu zolengedwa za 
mitundu iwiri, Anthu ndi ziwanda), 
kodi ndi Mtendere uti wa Mbuye 
wanu umene Mukuukana (kuti 
siWake?) 

14. Adalenga munthu 
kuchokera ku Dongo lolira monga 
ziwiya Zadongo, 

15. Ndipo adalenga ziwanda 
kuchokera Ku malawi a moto 
(wopanda utsi.) 

16. (Inu zolengedwa za 
mitundu Iwiri, anthu ndi ziwanda) 
kodi Ndimtendere uti wa Mbuye 
wanu Umene mukuukana (kuti 
siWake)? 

17. Mbuye wa kuvuma kuwiri 
Ndiponso Mbuye wa kuzambwe 
Kuwiri. 

18. (Inu zolengedwa za mitundu 
iwiri, Anthu ndi ziwanda), kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

19. Adaika nyanja ziwiri 
zokumana (Yamadzi amchere, ndi 
yamadzi Ozizira). 

20. Pakati pake pali 
chitsekerezo, Sizilowana; 



§32&&ak£ 6^\j 



>*^%;%ck\ 



h^ ( p£>&QZi\& 



%$&z£&&fy&> 



® t 



ytfivK" ?,\ A < 



!^u^o>W 



hgtj£i\&» 5<^£Jlcy 



tysptdfySp"*' 






Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1160 



TV t£-\ 



o* j*J\i jy * 



21. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri, Anthu ndi ziwanda), kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene mukuukana (kuti siWake?) 

22. M'menemo mumatuluka 
ngale Zing'onozing'ono ndi ngale 
Zikuluzikulu. 

23. (Inu zolengedwa za mitundu 
iwiri, Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

24. Ndipo (lye) ali nazo zombo 
(Zimene zapangidwa ndi manja 
Anu), zoyenda panyanja, 
zazikuluzikulu Ngati mapiri. 

25. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri, Anthu ndi ziwanda), kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

26. Zonse zili pamenepo 
(padziko) Nzakutha. 

27. Ndipo idzatsala nkhope ya 
Mbuye wako Mwini ulemerero ndi 
mtendere; 

28. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

29. (Onse) akumwamba ndi 
pansi Akupempha lye (zofuna 
zawo)! Tsiku lililonse lye 
ngotanganidwa (Kupatsa uyu 
ulemerero, ndi Kutsitsa uyu). 



vsrit'-fc' ^w«/r< 



#^»V4^J 



%&\;99m&& 









Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1161 



rv ^j*-i 



$hj\ijf* 



30. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri, Anthu ndi ziwanda), kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

31. Posachedwapa (patsiku la 
chiweruzo), Tidzaikapo mtima (pa 
chiwerengero Chanu (cha zochita 
zanu) inu anthu ndi Ziwanda. 

32. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

33. E, inu ziwanda ndi anthu! 
ngati Mungathe kutuluka 
m'mphepete mwa Thambo ndi 
nthaka (pothawa Mulungu), 
Tulukani! Simungathe kutuluka 
Pokhapokha ndi mphamvu. (Koma 
inu Simungathe kutero.) 

34. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siwake?) 

35. Mudzathiridwa malawi 
amoto ndi Mtovu wamoto 
wosungunuka ndipo Simungathe 
kudziteteza ku chilango Chimenechi. 

36. (Inu zolengedwa za mitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

37. (Kumbuka) pamene thambo 
Lidzang'ambika ndi kukhala 



®y$^$tife 



$&&#&£ 



.imte^ifc 



' u*'\ 






$k3^Jt&&K&&Z 



% 



)js*±> 



<^m>M% 



%%a&%&<j®($ 



Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1162 



rv>>i 



00 j*J\ hr* 



Lofiira ngati chikopa chofiira 
(Kapena ngati mafuta oyaka), 

38. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

39. Ndipo patsikulo 
(long'ambidwa thambo), Munthu 
ndi chiwanda, sadzafunsidwa Za 
tchimo lake, 

40. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

41. Adzadziwika oipa (pakati pa 
anthu Ndi ziwanda) ndi zizindikiro 
zawo (Zowazindikiritsa) .Ndipo 
Adzagwidwa maliombo awo ndi 
Mapazi awo (ndi kuponyedwa Ku 
Jahena). 

42. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

43. (Kudzanenedwa 
mowadandaulitsa): Iyi ndi 
Jahannama yomwe adali Kuitsutsa 
oipa. 

44. Adzakhala akuyenda pakati 
pa moto Ndi pakati pa madzi 
owira, Otentha kwambiri. 

45. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 



S^jtf 



©c#^»<& 



^^&&®^£ 



€^t#»$ 






^m^&> 



%£^%^$if&*$> 



^^®%tiSK 



®,±w\''<<X\\,<\< 



#^v&*: 



Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1163 



XV ftji-i 



^^'^ 



Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

46. Koma amene waopa kuti 
adzaimitsidwa kwa Mbuye wake 
(pa nthawi yachiweruzo). 
Adzalandira minda iwiri (Yaikulu 
yamtendere). 

47. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

48. (Minda ya mitengo) 
yanthambi Zofwanthamuka. 

49. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

50. M'menemo muli akasupe 
awiri, omwe Akuyenda. 

51. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

52. M'menemo muli zipatso za 
mtundu Uliwonse, mitundu iwiri 
iwiri. 

53. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

54. Atatsamira pa zoyala, mkati 
mwake Mosokerera veleveti 



£ i 



*&&&&%# 



$$BC#»9${ 



\>* 



wtetsritii 






®«y?l3;&#j e^»££jtj 



q$a#s»$ 



*#£W?JS f e$c&&&' 



Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1164 



TV *j*-l 



j*J\9jy* 



wochindikala; Ndipo zipatso 
zam'minda iwiriyi Nzapafupi 
(kuzithyola). 

55. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

56. M'mindamo muli akazi 
oyang'ana Amuna awo okha basi, 
mawuthu, Omwe sadakhalepo 
malo amodzi ndi Munthu kapena 
chiwanda Asadakumane ndi iwo. 

57. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

58. Kukongola kwake 
(akaziwo) kuli Ngati ngale 
zikuluzikulu ndi 

Zing ' onozing ' ono . 

59. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

60. Malipiro a ntchito zabwino 
Ndikulandira zabwino basi. 

61. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

62. Ndipo kuonjezera paminda 
iwiri (Ija) palinso minda ina iwiri. 



>&& 



«MjS^3t$ 






%$®%>8>m 



&$%&$§% 



«$BML$®($4 









Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1165 *V *>i 



dd J^SjJ-* 



63. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

64. Yobiriwira, kwambiri. 

65. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

66. M'menemo muli akasupe 
awiri Ofwamphuka madzi 
mwaphamvu. 

67. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

68. Mmenemo muli zipatso: 
mitengo Yakanjedza ndi 
yamikangaza. 

69. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

70. M'menemo muli akazi 
amakhalidwe Abwino, owala 
nkhope; 

71. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

72. Okongola maso; achikhalire 
M'mahema awo; (Inu zolengedwa 



fySU&$9$i 



- ifa' 






©ttj&*5<^££$£ 



v*£Vfc,' «u:u 



fcMOMCW 



©6B338*3S£& 



\tm^m 



**'•*&&&& 



m&swi 






Surat 55. Ar-Rahman Juzu 27 



1166 



TV*>1 



00 c» 5 JJ- 



zamitundu iwiri Anthu ndi 
ziwanda) kodi ndi Mtendere uti wa 
Mbuye wanu umene Mukuukana 
(kuti siwake?) 

73. (Inu zolengedwa za mitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
mtendere Uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake)? 

74. Amene sadakhalepo malo 
amodzi Ndi munthu kapena 
chiwanda Asadakumane ndi iwo; 

75. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

76. Uku atasamira misamiro 
yawofuwofu Yokutidwa ndi 
zobiriwira; ndi Zoyala zokongola, 
zakapangidwe Kodabwitsa. 

77. (Inu zolengedwa zamitundu 
iwiri Anthu ndi ziwanda) kodi ndi 
Mtendere uti wa Mbuye wanu 
umene Mukuukana (kuti siWake?) 

78. Latukuka ndi kudalitsika 
dzina La Mbuye wako Mwini 
ulemerero Ndi ufulu. 






m%$& 



®J$%$^H>aU 




Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 



1167 



TV $->! 



1 4*31 jji Ojj-*» 




SURAT AL-WAQPAH LVI 




Surayi yayamba ndi nkhani yofotokoza zakudza kwa tsiku 
lachiweruzo ndi zoopsa zimene zidzatsagana nalo. Kenako 
yafotokoza kuti anthu patsiku limenelo adzakhala m'mitundu 
itatu. Ndipo yalongosola mwatsatanetsatane za mtundu uliwonse 
ndi zomwe mtunduwo wakonzeredwa zolingana ndi ulemerero 
wake, kapena chilango cholingana ndi uchimo wake ndiponso 
kunyoza kwake. 

Kenako yalongosola momveka zizindikiro za mtendere wa 
Mulungu, ndi zizindikiro za mphamvu Zake zoposa 
pakalengedwe ka anthu, mbewu, madzi ndi moto, ndi kuti 
potsatira pazimenezi pakhale kulemekeza Chauta. Ndipo Surayi 
yalumbira kuti Qur'ani njolemekezeka ndi kudzudzula 
osakhulupirira pa machitidwe awo oipa pakutsutsa kwawo 
mmalo mothokoza. Komanso yalongosola mwatsatanetsatane za 
mitunduyo, mtendere kapena moto. 

Surayi yamaliza ndi kutsimikiza kuti chilichonse 
chatchulidwa m'suramo ndi choonadi. Ndipo yalamula 
zakulemekeza Mulungu. 




Siirat 56. Al-Waqi'ah Juzu27 I H68 I tV>>i o*\ m «A\J\ 5j>- 



SuratAl-Waqi'ahLVI 

M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 



1. Chikadzapezeka 
chopezekacho (Chiweruzo), 

2. Palibe wotsutsa za kupezeka 
kwake. 

3. Chidzatsitsa (oipa) ndi 
kutukula (Abwino); 

4. Nthaka ikadzagwedezeka 
kwamphamvu, 

5. Ndipo mapiri 
akadzaperedwaperedwa, 

6. Nkukhala fumbi longouluka, 

7. Choncho, inu mudzakhala 
m'magulu Atatu (kulingana ndi 
zochita zanu). 

8. Anthu akumanja (abwino;) 
taonani Kukula kwa ulemerero wa 
anthu Akumanja! 

9. Ndi anthu akumanzere (oipa;) 
taonani Kuipa khalidwe la Anthu 
akumanzere! 

10. Ndipo otsogola (pochita 
zabwino padziko) Adzakhalanso 
otsogola (polandira Ulemu tsiku 
lomaliza). 

11. Iwowo ndioyandikitsidwa 
(kwa Mulungu). 

12. M'minda yamtendere. 



-fX*. ■ < 



mm 






O^tfc^l^ 






**'•&•"' 






Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 1 169 X V *>•» o 1 tft jit 3jj~, 



13. (I wo wo oyandikitsidwawo), 
gulu lalikulu Lochokera 
kumibadwo yakale. 

14. Ndipo ochepa ochokera ku 
mbadwo Wotsirizira. 

15. Uku ali m'makama 
(m'mabedi) Olukidwa ndi zingwe 
zagolide, 

16. Atatsamira m'makamawo 
uku Akuyang'anizana 
(mwachikondi). 

17. Anyamata osasintha 
adzakhala Akuwazungulira iwo 
(Ndi kuwatumikira). 

18. Uku atatenga matambula 
ndi maketulo (Odzazidwa ndi 
zakumwa za ku Janat), Ndi 
zipanda zodzazidwa ndi zakumwa 
Zochokera mu akasupe oyenda; 

19. (Zakumwa zake) 
Zosapweteketsa mutu Ndiponso 
zosaledzeretsa; 

20. Ndi zipatso 
(zamitundumitundu) Zimene 
azikazisankha; 

21. Ndi nyama yambalame 
imene mitima Yawo izikafuna; 

22. Ndi akazi ophanuka Maso 
mokongola, 

23. (Kukongola kwawo) ndiye 
ngati ngale Zosungidwa bwino 
mzigoba zake. 






®&M&<&&$ 



*£&&&$&> 






Surat 56. Al-WaqFah Juzu 27 1 170 Y V pjk-\ o*\ ** jii ojj- 



24. Kukhala mphoto chifukwa 
Chazimene amachita (zabwino 
Padziko lapansi). 

25. M'menemo sakamva mawu 
achabe Ngakhale nkhani yamachimo, 

26. Koma mawu oti: 
"Mtendere! Mtendere!" 

27. Anthu akudzanja lamanja. 
Taonani Kukula malipiro a anthu 
akudzanja Lamanja! 

28. (Adzakhala m'mithunzi ya) 
mitengo Ya masawo yopanda minga. 

29. Ndi mitengo ya nthochi 
yobereka Kwambiri. 

30. Ndi m'mithunzi 
yotambasuka Kwambiri, yosachoka, 

31. Ndi madzi oyenda 
mosalekeza, 

32. Ndi zipatso zambiri, 

33. Zopezeka nyengo zonse, 
ndiponso Zosakanizidwa (kwa 
amene akuzifuna). 

34. Ndi zoyala zapamwamba 
(zawofuwofu) 

35. Ndithu, tidzawalenga (akazi 
Okhulupirira) m'kalengedwe 
Kapamwamba. 

36. Tidzawapanga kukhala 
anamwali. 

37. Okondedwa ndi amuna awo; 
Ofanana misinkhu, 



*$&&&$£ 






$&M 












®m&& 



Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 1171 Y V * >i ^ &\J\ oj^. 



38. Aanthu akudzanja la manja. 

39. Gulu lalikulu lochokera ku 
mibadwo Yakale. 

40. Ndiponso gulu lalikulu 
lochokera ku M'badwo wotsiriza. 

41. Anthu akudzanja 
lakumanzere. Taonani chilango 
choopsa Kwa anthu akudzanja 
lakumanzere! 

42. Adzakhala mumvuchi 
wamoto Ndi m'madzi owira. 

43. Ndi mumthunzi wa utsi 
wakuda. 

44. Siwoziziritsa ndiponso 
Siwosangalatsa. 

45. Ndithu, iwo amakhala 
kalelo Mosangalala (samalabadira 
kumvera Mulungu), 

46. Ndipo amapitiriza kuchita 
machimo Aakulu (polinga kuti 
palibe Kuuka ku imfa). 

47. Ndipo amanena (motsutsa): 
"Kodi Tidzaukitsidwa tikadzafa, 
thupi lathu Litasanduka fumbi ndi 
mafupa (ali Ofumbwa), 
tidzabwezedwanso Ku moyo 
wachiwiri? 

48. Kodi ndi makolo athu akale 
( Adzaukitsidwanso ! )" 

49. Nena kwa iwo (poyankha 
kutsutsa Kwawo). Ndithudi, 









Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 1 172 TV^i on h&\J\ ojj- 



amibadwo Yoyamba ndi mibadwo 
yomaliza omwe Inu muli m'gulu 
lawo, 

50. Adzasonkhanitsidwa 
m'nthawi Ya tsiku lomwe 
lakhazikitsidwa. 

51. Kenako inu osokera (njira 
Yachilungamo), otsutsa (za kuuka,) 

52. Mudzadya (ku Jahena) 
mtengo wa Zakkum, (mtengo 
wowawa wopezeka Mu Jahena). 

53. Mudzakhutitsa mimba zanu 
ndi Umenewu (chifiikwa cha njala 
Yadzaoneni). 

54. (Mkhuto wa mtengowo) 
adzamwera Madzi owira; 

55. Adzamwa monga mmene 
imamwera Ngamira yodwala 
matenda aludzu! 

56. Hi ndi pwando lawo tsiku 
lamalipiro. 

57. Ife tidakulengani Kodi 
nchifukwa ninji 
Simukukhulupirira? 

58. Tandiuzani za madzi 
(ambewu ya Munthu) amene 
mumawathira M'chiberekero, 

59. Kodi inu ndiamene 
mumawalenga (Madziwo ndi 
kumayang'anira Mkusinthasintha 
kwake kuti akhale Cholengedwa) 












®&^£0i& 



$G&J^ 






Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 1 173 TV * >i 



0*\ 4*31 jil Ojj^i 



kapena Ife ndiAmene 
Timawalenga? 

60. Ife tidalamula imfa pakati 
panu ndipo Ife sitili wolephera, 

61. Kubweretsa ena m'malo 
Mwanu ndi kukulengani 
Mwamaonekedwe ena omwe 
Simumawadziwa. 

62. Ndipo ndithu,mukudziwa 
kalengedwe Koyamba; nanga 
bwanji simukuganiza. 

63. Tandiuzani za zimene 
mukubzala? 

64. Kodi ndinu amene 
mukuzimeretsa Kapena Ndife 
Amene tikuzimeretsa? 

65. Tikadafuna 
tikadazitembenuza (Mbewu 
zimenezo kukhala zouma 
Isanakwane nthawi yake 
yozithyola) Choncho mukadakhala 
mukudandaula. 

66. (Uku mukunena:) "Ndithu, 
ife tili M'mangawa; 

67. Koma Ife tamanidwa 
(phindu la Khama lathu)." 

68. Kodi mukuwaona madzi 
amene Mukumwa! 

69. Kodi ndinu amene 
mudawatsitsa Ku mitambo kapena 
Ndife Amene Timawatsitsa? 









S&rjflb 









Surat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 I 1174 I YV *>i 01 4*31^1 Sjj- 



70. Tikadafuna tikadawapanga 
Kukhala amchere; nanga 
Nchifukwa ninji Simuthokoza? 

71. Kodi mukuwuona moto 
umene Mumaukoleza? 

72. Kodi ndinu amene 
mudameretsa Mitengo yake 
kapena Ndife tidaipanga? 

73. Ife taupanga kuti ukhale 
chikumbutso (Chamoto watsiku 
lomaliza akauona), Ndikuti ukhale 
chothandiza kwa anthu Apaulendo 
(amene akuyenda M'chipululu). 

74. Choncho, pitiriza 
kulemekeza Dzina la Mbuye Wako 
Wamkulu. 

75. Ndikulumbirira 
motsimikiza, mmene Mumatsikira 
nyenyezi (pomwe Zikulowa), 

76. Ndithu, kulumbira uku, 
mukadakhala Olingalira, 
nkwakukulu kwabasi (Pazimene 
kukusonya). 

77. Ndithu, iyi ndi Qur'an 
yolemekezeka (Ndipo mkati 
mwake muli zithandizo Zambiri). 

78. Idachokera mu buku 
lotetezedwa; 

79. Salikhuza kupatula okhawo 
oyeretsedwa (Angelo). 

80. Chivumbulutso chochokera 
Kwa Mbuye wa zolengedwa zonse. 



©&%&9pZ&\><&?$&>) 



6©j3##ij&!ftK 









§tim^ 



@JJ^I^J»iuAx-* 



)^s^0!Cyj^U fO~A 



^i^i^ 



®frS£&PA*& 



&&®m 






Siirat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 1 175 Y V *>» 



o*\ **3\jl\ 5jj-» 



81. Kodi kuitsutsa (Qur'an) 
nkhani iyi, Inu mukuinyozera? 

82. Kodi mwakuchita kukanira 
kukhala Kuthokoza kwanu pa 
Zimene wakupatsani? 

83. Kodi bwanji (mzimu wa 
mmodzi wa inu) Ukafika kummero 
(Panthawi ya imfa), 

84. Uku inu panthawi imeneyo 
mukuona Zimenezo, 

85. Pomwe Ife tili pafupi ndi 
iye Kuposa inu, koma inu 
simuona, 

86. Mukadakhala kuti 
simuzalipidwa (Pa zomwe 
mukuchita) 

87. Bwenzi mukuubweza 
(mzimuwo) ngati Mukunena zoona. 

88. Ngati (amene yamfikira 
imfayo) adali Mmodzi wa 
woyandikitsidwa (kwa Mulungu;) 

89. Kobwerera kwake ndi 
kumpumulo Ndi kumtendere ndi 
kupatsidwa Zonunkhira ndiponso 
Munda wa Mtendere. 

90. Ndipo ngati adali mmodzi 
wa anthu Akudzanja lamanja, 

91. (Kudzanenedwa kwa iye:) 
"Mtendere Ukhale pa iwe, amene 
udali m'gulu La anthu akudzanja 
lakumanja (Anthu abwino)." 









**&&&&& 






Siirat 56. Al-Waqi'ah Juzu 27 11761 * V *>i 



o*v Zf&\j)\ 5jj-*» 



92. Koma ngati adali Mmodzi 
wa anthu Otsutsa, osokera, 

93. Phwando lamadzi owira 
(ndilake), 

94. Ndi kupsa m'moto wa 
Jahena. 

95. Ndithu, izi (zatchulidwa 
m'surayi) Ndizoona; 
zotsimikizika. 

96. Choncho lemekeza dzina la 
Mbuye wako Wamkulu. 



9 '&*'\ 9 £ 6 



k^ffiOpjAfir* 




Siirat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1177 TVtji-l OV JUJLi-l Ojj^. 




Surayi yayamba ndikufotokoza kuti zonse zakumwamba ndi 
zapansi zimalemekeza Mulungu ndi kumyeretsa pamakhalidwe 
osayenerana ndi ulemerero Wake. Ndi kunena kuti Mulungu ndi 
Mwini wa zonse zakumwamba ndi zapansi. Ndi kutinso akudziwa 
bwinobwino zam'menemo ndi kuzichita mmene angafunire. 

Kenako surayi yalamulanso zakukukhulupirira mwa Mulungu 
ndi kupereka chuma panjira Yake. Ndipo yalongosola kusiyana 
kwa ulemerero wakupereka chuma panjira ya Mulungu 
chifukwa cha kusiyana zifukwa zoperekerazo. 

Ndiponso yasonyeza maonekedwe pa tsiku lachiweruzo a 
okhlupirira pamene kuunika kwawo kudzawatsogolera patsogolo 
pawo ndi m'mbali mwawo. Ndipo yasonyezanso maonekedwe a 
achinyengo pamene iwo azikapempha okhulupirira kuti awadikire 
ndi kuwagawirako kuunika kwawo. Koma pakati pawo padzaikidwa 
mpanda wokhala ndi khomo; mbali yamkati mwake muli chifundo 
cha Mulungu, ndipo mbali yakunja kwake kuli chilango cha Chauta. 

Komanso surayi yalimbikitsa okhulupirira kuti akumbukire 
Mulungu ndi kudzichepetsa pa choonadi chimene chavumbulutsidwa. 
Ndipo ikuwonetsanso ulemerero wa okhulupirira achimuna ndi 
achikazi kwa Mbuye wawo, ndi kobwerera kwa osakhulupirira 
otsutsa, ku Jahena. Ndipo kenako Surayi yapereka fanizo 
lakunyozeka kwa dziko lapansi ndi zonse za m'dziko, ndi ukulu 
wa tsiku lomaliza ndi zonse zili m'menemo. Ndipo ikupempha 
kuti tichite changu pofunafuna chikhululuko cha Chauta 
ndiponso ikutonthoza mitima pachinthu chilichonse chomwe 
chimaupeza mtima: chabwino kapena choipa, ponena kuti 
chilichonse, chabwino kapena choipa chidalembedwa m'buku 
kwa Mulungu; potero kuti munthu agonjere chiweruzo cha Chauta. 

Surayi yafotokozanso za kutumizidwa kwa aneneri ndi 
kutsatizana kwawo uku atalimbikitsidwa ndi zizizwa, mabuku 
ndi zina zowapatsa mphamvu kuti agwire ntchito ya ulaliki kuti 
anthu akhale molungama. 

Ndipo pomaliza surayi yapempha Asilamu kuti aope 
Mulungu. Ndipo yawalonjeza za chifundo chambiri chomwe 
palibe angachidziwe koma Mulungu yekha. 



Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1178 



YV*>l 



OV OjO^I 5jj-» 



Surat Al-Hadid LVII 



^ -■t jv^ — r j?v l- ^- — ^g= 



^M£ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Chilichonse chakumwamba 
ndi Chapansi chikulemekeza 
Mulungu (Ndi kumyeretsa 
kumakhalidwe Opunguka) ndipo 
lye ndiMwini Mphamvu, Wanzeru. 

2. Ufumu wakumwamba ndi 
pansi, Ngwake amapereka moyo 
ndi imfa. Ndipo lye 
Ngwamphamvu pa Chilichonse. 

3. lye alibe chiyambi; (adalipo 
Chilichonse chisadayambe); 
Wamuyaya, (zonse zikazatha); 
Woonekera (mzisonyezo pachinthu 
Chilichonse), wobisika mkati 
Kwambiri, (saonedwa ndi maso 
Pamoyo uno) lye Ngodziwa 
Chilichonse (kunja ndi mkati 
mwake). 

4. lye ndiAmene adalenga 
kumwamba Ndi pansi (ndi zonse 
zam'menemo) M'masiku asanu 
ndi limodzi Ndipo kenako 
adakhazikika Pampando Wake 
wachifumu (monga Momwe lye 
adziwira polongosola Ufumu 
Wake). Akudziwa Chilichonse 
cholowa m'nthaka ndi Chimene 
chikutuluka m'menemo; ndi 
Chilichonse chimene chikutsika 



o^ifc^JMki, 



"***- 



JK^feWPA^ 



wm 









Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1179 



YV*>1 



OV JbJLM djj*- 



Kumwamba ndi chimene 
chikukwera Kumeneko.Ndipo lye 
ali nanu paliponse Pamene muli. 
Ndithu, Mulungu Amaona 
chilichonse chimene Mukuchita, 
(sichibisika chilichonse Kwa lye). 

5. Ufumu wakumwamba ndi 
pansi Ngwake Ndipo kwa 
Mulungu nkobwerera zinthu (Za 
zolengedwa zake). 

6. Usiku amawulowetsa mu 
usana, Ndipo usana amawulowetsa 
Mu usiku. (Choncho kumasiyana 
Kutalika kwake); ndipo lye 
Ngodziwa Zobisika za m'zifuwa 
(ndi zoganiza Za m'mitima). 

7. Khulupirirani mwa Mulungu 
ndi Mthenga Wake, ndipo perekani 
(Panjira ya Mulungu m'chuma 
chimene Mulungu wakupatsani 
kuchiyang'anira. Choncho mwa inu 
amene akhulupirira (Mwa Mulungu 
ndi mthenga Wake) Ndikupereka 
(zimene awapatsa) iwo ali Ndi 
malipiro aakulu (kwa Mulungu) 

8. Kodi nchifukwa ninji 
simukhulupirira Mwa Mulungu 
pomwe Mneneri Akukuitanani kuti 
mukhulupirire Mbuye wanu (ndi 
kukulimbitsani pa Zimenezo) 
chikhalirecho (lye) Adalandira 
lonjezo lanu, (muli Mumsana wa 
atate wanu Adamu Kuti 
mdzakhulupirira,) ngati mulidi 
Okhulupirira. 



£}M&<JM^\m$ 



<%8\ 












Siirat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1180 



tV^i 



OV -UJL^I Ojj-* 



9. lye ndiAmene 
akuvumbulutsa kwa Kapolo Wake 
aya (ndime) zafotokoza 
Mwatsatanetsatane kuti akutulutseni 
Mum'dima (wa kusokera) ndi 
kukuikani Ku chiongoko cha 
kuunika. Ndipo ndithu, Mulungu 
Ngoleza kwa inu, Ngwachisoni. 

10. Kodi ndichifukwa chiani 
Simukupereka panjira ya Mulungu 
(Chuma chanu) pamene Mulungu 
Ndimwini wa zosiyidwa zonse 
Zakumwamba ndi zam'dziko 
lapansi. Sali ofanana mwa inu 
amene adapereka Chuma (panjira ya 
Mulungu) pamodzi Ndi kumenya 
nkhondo usadagonjetsedwe 
Mzinda wa Makka, iwowo 
ndiomwe Ali ndi ulemerero 
waukulu kuposa Amene apereka 
chuma chawo ndi Kumenya 
nkhondo pambuyo. Koma Onsewo 
Mulungu wawalonjeza zabwino 
(Ngakhale ali osiyana ulemerero 
wawo); Ndipo Mulungu akudziwa 
zonse zimene Muchita. (Choncho 
aliyense Adzalipidwa molingana 
ndi zimene Amachita). 

11. Kodi ndani wokhulupirira 
amene Angamkongoze Mulungu 
ngongole Yabwino kuti 
amuonjezere (zambiri) Malipiro 
ake? Ndipo iye Adzalandira 
malipiro aulemu (Pa tsiku 
lachiweruzo.) 












Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1181 



rv *>i 



OV JUJU-I 5jj^ 



12. Tsiku limene udzaona 
okhulupirira Achimuna ndi 
achikazi Kukutsogolera kuunika 
kwawo Patsogolo pawo ndi 
chakumanja kwawo (Uku angelo 
akunena kwa iwo): "Chisangalalo 
chanu lero ndi minda Imene pansi 
pake pakuyenda mitsinje. 
(Simdzatuluka) m'menemo mpaka 
Muyaya! Kumeneku ndiko 
Kupambana kwakukulu (kwa inu). 

13. Tsiku limene achinyengo 
achimuna ndi Achinyengo achikazi 
adzauza okhulupirira (Kuti:) 
"Tidikireni kuti tipeze Kuunika 
kwanu!" Kudzanenedwa 
(Mwachipongwe): "Bwererani 
pambuyo Panu mukafune kuunika 
kumeneko!" Ndipo padzaikidwa 
mpanda pakati pawo (Okhulupirira 
ndi achinyengo) Umene udzakhala 
ndi khomo, mkati Mwa 
mpandawo, (komwe ndi kumbali 
Ya ku Jannat) muli chifundo ndi 
Mtendere; kunja kwake, (komwe 
ndi Kumbali yamoto), kuli 
mazunzo Ndi chilango. 

14. (Achinyengo) adzaitana 
okhulupirira Ponena kuti: "Kodi 
sitidali nanu limodzi (Padziko ndi 
kumatsagana nanu?" 
(Okhulupirira) adzati: "Inde! 
(Mudali Nafe monga momwe 
mukunenera). Koma Inu 
munadziononga nokha ndipo 












$&&\ 






^sfiwy*^ sy "' "— 






Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1182 



rv ftjJt-i 



OV JbJj-l djj~- 



Mumayembekezera (kuti 
okhulupirira Awapeze mavuto ndi 
kuonongeka); Mudakaikira (zinthu 
za chilengedwe Chanu); choncho 
zikhulupiriro zanu Zonama 
zidakunyengani pomwe mudali 
Angwiro mpaka lamulo la 
Mulungu (imfa) Lidakupezani, 
komanso adakunyengani Onyenga 
(satana) za Mulungu. 

15. Basi lero sililandiridwa dipo 
Lochokera kwa inu (limene 
Mungalipereke kuti 
mudzipulumutse Ku chilango 
ngakhale likhale Lamtengo 
wotani). Ndiponso Sililandiridwa 
dipo lochokera kwa Osakhulupirira 
(amene adalingana nanu 
N'kusakhulupirira kwawo 
Mulungu) Malo anu nonsenu ndi 
kumoto basi. Amene wa ndi malo 
okuyenerani. Kumeneko ndiko 
kobwerera koipa Kwabasi! 

16. Kodi siidayandikire nthawi 
kwa Okhulupirira kuti mitima 
yawo Idzichepetse pokumbukira 
Mulungu Ndi zomwe 
zidavumbulutsidwa za Chowonadi 
(Qur'an yolemekezeka)? Ndi Kuti 
asakhale monga omwe 
adapatsidwa Buku kale (Ayuda ndi 
Akhrisitu) Amene nthawi yawo 
yosiyana ndi Aneneri awo idali 
yaitali. Choncho mitima yawo 
idauma ndipo Ambiri aiwo adatuluka 
m'chilamulo (Cha Mulungu). 









'}$&'jn$3W$ 



©jL^Jl 






©■ 



IjyL* 



Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 I H83 I rv s-ji-^ oV Jb>M 5j_^ 



17. Dziwani kuti Mulungu 
amaukitsa Nthaka itauma 
(poitsitsira mvula kuti Mmera 
umere) . Choncho 

Takulongosolerani zisonyezo kuti 
inu Mukhale ndi nzeru. 

18. Ndithu amene akupereka 
sadaka, Amuna ndi akazi, ndi 
kumamkongoza Mulungu ngongole 
yabwino (Mulungu) Adzawaonjezera 
malipiro pa zimenezi. Ndipo ali 
ndi malipiro aulemu 

19. Ndipo amene akhulupirira 
Mulungu Ndi aneneri Ake, iwowo 
ndiwo oona (Pa chikhulupiriro); 
ndi ofera panjira ya Mulungu 
(onsewo) azapeza malipiro Awo 
ndi kuwala kwawo kwa Mbuye 
Wawo. Koma amene 
sadakhulupirire Ndi kutsutsa 
zisonyezo Zathu Iwowo ndi eni a 
ku Jahena. 

20. Dziwani kuti ndithu, moyo 
wapadziko Lapansi ndimasewero, 
wachabe Chokometsera chabe, 
Chonyadiritsana pakati Panu 
(paulemerero) ndi kuchulukitsa 
Chuma ndi ana (pomwe zonsezo 
Sizikhala nthawi yayitali;) fanizo 
lake Lili ngati mvula yomwe 
mmera wake Umakondweretsa 
alimi; kenako Umauma, ndipo 
uuona uli wachikasu; Kenako 
nkukhala odukaduka 
(Oonongeka).Koma tsiku lomaliza 















Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1184 



TV*>» 



OV JbJL^t djj-*. 



kuli Chilango chaukali; ndi 
chikhululuko Komanso chikondi 
chochokera kwa Mulungu.Moyo 
wapadziko lapansi suli Kanthu, koma 
ndichisangalalo Chonyenga basi. 

21. Chitani changu (pa zinthu 
Zokupatitsani) chikhululuko 
chochokera Kwa Mbuye wanu ndi 
munda wa Mtendere womwe 
mulifupi mwake Muli ngati 
kutambasuka kwa kumwamba Ndi 
pansi; wakonzedwera amene 
Akhulupirira Mulungu ndi aneneri 
Ake; Umenewo ndi ubwino wa 
Mulungu Womwe akuupereka kwa 
amene Wamfuna. Mulungu Ndi 
Mwini ubwino waukulu. 

22. Silipezeka tsoka lililonse 
panthaka (Monga chilala) ngakhale 
pamatupi Anu koma lidalembedwa 
kale m'Buku (La Mulungu) 
tisadalilenge ndi Kulipereka. 
Ndithu zimenezo Kwa Mulungu 
nzofewa. 

23. (Takudziwitsani zimenezi) 
kuti Musadandaule ndi chimene 
Chakudutsani, ndi kutinso 
Musakondwere monyada ndi 
chimene Wakupatsani. Mulungu 
sakonda Aliyense wodzitama, 
wonyada, 

24. Amene akuchita umbombo 
(ndi chuma Chawo; ndipo 
osapereka panjira ya Mulungu) ndi 
kumalamula anthu ena Kuchita 















Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1185 



tY*>i 



OV OjOJ-I O^j- 



umbombo ndipo amene 
Atembenuke (adzalandira chilango 
Chachikulu), ndithu,Mulungu 
Ngolemera, (sasaukira chilichonse 
Kwa wina);Ngotamandidwa. 

25. Ndithu, tidatuma aneneri 
Athu Pamodzi ndi zozizwitsa. 
Ndipo Tidavumbulutsa pamodzi 
ndi iwo mabuku Ndi muyeso wa 
choonadi kuti anthu achite 
Chilungamo. Ndipo tidalenga 
chitsulo Momwe muli mphamvu 
zambiri (pa Nkhondo) ndiponso 
chithandizo kwa anthu (Akakhala 
pa mtendere ndi kupindula Nacho 
pochita zowathandiza pa moyo 
Wawo). Ndi kuti Mulungu 
amuonetsere Poyera, amene 
angachiteteze (chipembedzo 
Chake) ndi aneneri Ake 
(Kupyolera m'chitsulocho) pomwe 
lye Sakumuona. Ndithu, Mulungu 
Ngwamphamvu (pa chilichonse) 
Ngopambana 

26. Ndipo ndithu tidatuma Nuhi 
ndi Ibrahim ndi Kukhazikitsa 
uneneri m'mbumba yawo Ndi 
mabuku (achiongoko). Ena mwa 
Iwo adayenda panjira yolungama, 
Koma ambiri a iwo adapatuka 
panjira Yolungamayo. 

27. Kenako tidatsatiza pambuyo 
Pawo ndi aneneri athu ndipo 
Tidasatiza ndi Isa mwana wa 
Mariamu, ndipo tidampatsa Injili 












Surat 57. Al-Hadid Juzu 27 



1186 



TV *jJfe-i 



OV JUJL^I Ojj-*» 



ndipo tidaika kufatsa Ndi chifundo 
m'mitima Ya omwe adamtsatira. 
Koma kusakwatira, 
Adakuyambitsa okha; 
Sitidawalamule zimenezo Koma 
(adayambitsa zimenezo) Chifukwa 
chofuna chikondi Cha Mulungu; 
koma Sadazisunge moyenera. 
Choncho amene adakhulupirira 
Pakati pawo tidawapatsa Malipiro 
awo, koma Ambiri a iwo ngolakwa 

28. E, inu amene 
mwakhulupirira! Opani Mulungu, 
Ndipo khulupirirani Mthenga 
Wake, Akupatsani zigawo ziwiri 
za chifundo Chake. Ndipo 
akupangirani kuunika koongoka 
nako (Poyenda patsiku 
lachiweruzo.) Ndiponso 
Akukhululukirani ndipo Mulungu 
Ngokhululuka mochuluka 
kwambiri, Ngwachisoni. 

29. (Mulungu akupatsani 
zonsezi) kuti Adziwe amene 
adapatsidwa Buku (omwe 
Sadamkhulupirire 
Mtumiki{SAW}) kuti iwo 
Sangathe kudzisankhira okha 
chilichonse Mumtendere wa 
Mulungu. Ndipo ndithu, Ubwino 
wonse uli m'manja mwa Mulungu 
Yekha.Amapatsa amene wamfuna 
mwa Akapolo ake. Ndipo 
Mulungu ndi Mwini Ubwino 
wochuluka. 






'*l, U 99** 






w&^ss&j^£ 



%sw« 






^ ,-^t 



Surat 58. Al-Mujadilah Juzu 28 



1187 



tA*>l 



OA A^l^l Ojj-j 




Surayi yayamba ndikufotokoza nkhani ya mkazi amene 
adasalidwa ndi mwamuna wake. Ndi za lamulo losala mkazi. 

M'sura imeneyi Mulungu wanena m'ndime zochulukirapo za 
amene amada chipembedzo Chake ndi kuwachenjeza za 
kunong'onezana za machimo ndi mtopola. Ndipo wawaongolera 
Asilamu kumwambo wonong'onezana pakati pawo, ndi pakati 
pa Mneneri (madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndi iwo. 
Ndipo kenaka surayi yapitirira ndi kudzudzula achinyengo 
m'kuyanjana kwawo ndi osakhulupirira ndi kuwatcha kuti ndi 
eni chipani cha satana; otaika. Ndipo yamaliza ndi kusimba 
khalidwe loyenera kukhala nalo okhulupirira; kumene kuli 
kusankha chikondi cha Mulungu ndi Mneneri Wake (madalitso 
ndi mtendere zikhale naye) kuposa wina aliyense ngakhale 
atakhala bambo wawo, ana awo, abale awo, kapenanso akubanja 
lawo. Ndipo anthu otero yawatcha kuti ndi wo achipani cha 
Mulungu, chopambana. 




Surat58.Al-Mujadilah Juzu28 I H88 I *A *>i 



oA 4tal£i Sjj~» 



SuratAl-Mujadilah LVIII 



.w~ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndithu Mulungu wamva 
mawu a (amkazi) Amene 
akubwezeranabwezerana nawe 
(Mawu) pa za mwamuna wake 
(amene Adamsala); ndipo akusuma 
kwa Mulungu. Ndipo Mulungu 
akumva Kukambirana kwanu; 
Ndithu, Mulungu Ngwakumva 
Ngopenya (chilichonse). 1 

2. Amene akufanizira mwa inu 
(Asilamu) Akazi awo (ndi amayi 
awo) iwo siamayi Awo; amayi 
awo ndiamene adawabereka. 
Ndithu,iwo akunena mawu oipa 
ndi onama. Koma ndithu, Mulungu 
ali Wofafaniza (Machimo) ndi 
Wokhululuka (Amene walapa). 

3. Amene akuwafanizira akazi 
awo (ndi Amayi awo) kenako 
nkubweza zimene Adanena, 
apereke ufulu kwa kapolo 
Asanakhale malo amodzi (ndi 



mm 



^^* 









». 






Arabu adali ndi chizolowezi chakupatukana ndi mkazi. Izi zimachitika 
akanena mawu akuti: "Ndikukuyerekeza ngati mayi wanga." Choncho 
amangokhala naye mkazi uja, osamkhudza ndiponso osamulola kuti akwatiwe 
ndi mwamuna wina. Samamchitiranso zimene munthu amachitira mkazi wake 
monga kumveka ndi kumdyetsa. 

Msilamu wina adamsiya mkazi masiyidwe onga amenewa ndipo mkazi uja 
adapita kukakambirana naye Mtumiki (madalitso ndi mtendere zikhale naye). 
Choncho Chisilamu chidaletsa machitidwe onga amenewa. 



Surat 58. Al-M ujadilah Juzu 28 



1189 



YA*>I 



OA ibl^l djj~t 



mkaziyo). Amenewa ndi malamulo 
a Mulungu kwa Inu (amene) 
mukuchenjezedwa nawo. Ndipo, 
Mulungu akudziwa zimene 
Mukuchita (zoonekera poyera ndi 
Zosaonekera choncho sungani 
Malamulo amene Mulungu 
Wakhazikitsa pa inu). 

4. Ndipo amene sadapeze 
(kapolo) amange Miyezi iwiri 
yondondozana Asadakhalirane 
pamodzi (ndi mkaziyo), Koma 
amene sadathe kumanga adyetse 
Masikini makumi asanu ndi 
limodzi (60). Malamulo amenewa 
aikidwa kuti Mukhulupirire mwa 
Mulungu ndi Mthenga Wake. 
Amenewo ndiwo malire A 
Mulungu; (malamulo 
okhazikitsidwa Ndi Mulungu 
choncho musawalumphe). Ndipo 
chilango chopweteka chili pa 
Osakhulupirira. 

5. Ndithu, amene akutsutsana 
ndi Mulungu Kudzanso Mthenga 
Wake, ayalutsidwa Monga momwe 
adayalutsidwira amene adalipo 
Patsogolo pawo; ndithu 
tavumbulutsa aya Zolongosola, 
momveka (pa zololedwa ndi 
Zoletsedwa). Ndipo chilango 
Choyalutsa chili pa osakhulupirira. 

6. (Kumbuka) tsiku limene 
Mulungu Adzaukitsa akufa onse 
ndi Kuwafotokozera zimene 



<S&S» 









8^f*#wWi 



Surat58.Al-Mujadilah Juzu28 I H90 I tA *jju» 



OA ibbfcl djj^> 



adachita (Pa moyo wa dziko 
lapansi: zoipa ndi Zabwino; 
Mulungu) adazisunga Mozilemba 
koma iwo adaziiwala. Ndipo 
Mulungu ndi mboni wa zonse 
(Palibe chingabisike kwa lye). 

7. Kodi sukudziwa (iwe, 
womvera Wanzeru) kuti Mulungu 
akudziwa Zakumwamba ndi 
zam' dziko lapansi? Sipakhala 
manong'onong'o a (anthu) Atatu 
koma lye ngwachinayi wawo (Ndi 
kudziwa kwake kosabisirika 
Chilichonse cha kumwamba ndi 
M' dziko), ngakhale a (anthu) 
asanu Koma lye Ngwachisanu ndi 
chimodzi Wawo (mkudziwa 
Kwake), ngakhale ali ochepera 
kuposera pamenepa kapena 
Ochulukira koma lye Ali nawo 
paliponse pomwe ati akhale 
(Mulungu ali nawo pamodzi 
mukudziwa Kwake kosabisika 
chilichonse), kenako 
Adzawafotokozera pa tsiku 
lachiweruzo Zimene adachita; 
ndithu, Mulungu Ngodziwa 
chilichonse (mokwanira). 1 

8. Kodi sudaone! kwa amene 
aletsedwa Kunong'onezana zoipa 
pakati pawo, Kenako akubwereza 












M'ndime iyi, Mulungu akutichenjeza kuti pamene tikuchita kalikonse 
tisamaganizire kuti Mulungu sakutiona. Palibe chimene chingabisike kwa 
Mulungu cha m'dziko lapansi kapena kumwamba; m'zoyankhula kapena 
m'zochitachita. 



Surat58.Al-Mujadilah Juzu28 1191 I TA;>i 



OA ibbfcl djj^ 






zimene Adaletsedwa? 
Akunong'onezana za Machimo, 
mtopola ndi kunyoza Mtumiki. 
Akakudzera akukulonjera (Ndi 
malonje achinyengo) amene 
Mulungu sadakulonjerepo nawo 
ndipo Akunena m'mitima mwawo: 
"Kodi Nchifukwa chiyani 
Mulungu sakutilanga Ndi mawu 
tikunenawa (ngati iyeyu ndi 
Mtumikidi wa Mulungu?" 
Jahannama Ikuwakwanira: 
adzailowa. Ndipo Taonani kuipa 
malo (awo) wobwerera! 1 

9. E, inu amene mwakhulupirira! 
Ngati Mukunong'onezana, 
musamanong'onezane za Machimo 
ndi mtopola ndi kunyoza Mtumiki: 
Koma nong'onezanani za 
kulungama Ndi kuopa Mulungu 
ndipo muopeni Mulungu, Kwa lye 
nkumene mudzasonkhanitsidwe 
(ndi Kuweruzidwa). 

10. Ndithu, manong'onong'o 
oipa Amachokera kwa satana kuti 
Adandaulitse amene akhulupirira; 
Koma sangawapweteke nawo 
Chilichonse kupatula Mulungu 
atafuna Ndipo okhulupirira 
atsamire kwa Mulungu yekha, 
(asalabadire Zonong'onezana zawo) 



Ayuda amamlonjera Mtumiki ndi mawu akuti: "Saamu alayikumu" 
kutanthauza kuti: Imfa ikhale pa inu. Amayankhula mokhotetsa lirime kuti 
ampusitse Mtumiki kuti aganizire kuti akumlonjera moyenera kuti: "Asalamu 
alayikumu." 









Sfirat 58. Al-Mujadilah Juzu 28 



1192 



TAfr>» 



3 A iJibrl 5jj-j 



11. E, inu amene 
mwakhulupirira! Kukapemphedwa 
kwa inu kuti perekani Malo 
pabwalo (pokhala); perekani 
Malowo (kuti anzanu apeze 
pokhala; Mukatero) Mulungu 
akuphanulirani (Chifundo Chake 
pano padziko ndi 
Kumwamba).Ndipo kukanenedwa 
kuti Imirirani, muimirire 
(musanyozere, Apatseni ena malo); 
Mulungu Awakwezera (ulemerero) 
mwa inu Amene akhulupirira ndi 
amene Apatsidwa nzeru. Ndipo 
Mulungu Akudziwa bwino zimene 
mukuchita. 1 

12. E, inu amene 
mwakhulupirira! Mukafuna 
kuyankhula ndi Mtumiki(SAW) 
Tsogozani pazoyankhula zanuzo, 
Sadaka: kutero ndibwino kwa inu 
Ndiponso ndichoyeretsa (mitima 












1 Kuvumbulutsidwa kwa ndime iyi pali mawu akuti: Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) amaikira mtima kwambiri pa anthu amene adamenya 
nkhondo ya Badir; amgulu la Amuhajirina ndi Answari. 
Ndipo ena mwa iwowa adadza pa bwalo la Mtumiki ndi kupeza anthu ena 
atakhala kale Adakhala chiimire chifukwa chosowa pokhala uku 
akuyembekezera kuti anzawo aja awapatseko pokhala; koma anthu adakhala 
kale aja sadalabadireko chilichonse. Mtumiki ataona izi zidamuwawa 
mumtima ndipo adawauza omwe adakhala kale aja kuti aimirire apereke malo 
kwa anzawo. Amunafikina adayamba kum'dzudzula Mtumiki (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) kuti bwanji akuchotsa anthu okhalakhala pamalo 
chifukwa cha anthu obwera mochedwa; sikupanda chilungamo kumeneko? 
Adatero Amunafikina aja. Ndipo poyankha zimenezi Mulungu adati: "E, inu 
okhulupirira! Mukauzidwa kuti perekani malo kwa anzanu mupereke. Ndipo 
mukauzidwa kuti imirirani, muimirire." 

M'ndime imeneyi Mulungu akutiphunzitsa kuti timvere Mtumiki(SAW) pa 
chilichonse chimene watilangiza popanda kuwiringula. 



Surat 58. Al-Mujadilah Juzu 28 



1193 



ta*>i 



oA 4bl£i ojj-- 



yanu). Koma ngati simudapeze 
(sadakayo) Ndithu, Mulungu 
Ngokhululuka, Ngwachisoni. 

13. Kodi mwaopa kutsogoza 
sadaka Pakunena naye (Mtumiki)? 
Ngati Simudachite zimenezi basi 
Mulungu wakukhululukirani; 
Choncho pempherani swala 
moyenera Ndipo perekani zakaat 
Ndiponso mverani Mulungu 
pamodzi Ndi Mtumiki Wake. 
Ndipo Mulungu Akudziwa zonse 
zimene mukuchita. 

14. Kodi sukuwaona amene 
apalana ubwenzi Ndi anthu amene 
Mulungu Wawakwiira; iwo sali 
mwa inu Ndiponso sali mwa iwo. 
Ndipo Akulumbira zabodza uku 
akudziwa (Kuti limeneli 
ndibodza). 

15. Mulungu wawakonzera 
chilango Chaukali, ndithudi 
zimene amachita Nzoipa. 

16. Kulumbira kwawo 
adakuchita kukhala Chodzitetezera 
(iwo, ana Awo ndi chuma chawo); 
choncho Adatsekereza (anthu) ku 
njira ya Mulungu; ndipo chilango 
Choyalutsa chili pa iwo. 1 









$fc%ffl%&yfy!m 






Tanthauzo la "Kulumbira kwawo adakuchita chodzitetezera" ndiko kuti 
Amunafikina amadziteteza kwa Asilamu pakungosonyeza Ghisilamu 
chachiphamaso, chapakamwa pokha pomwe mitima yawo siimakhulupirira. 
Amatero pakuopa kuti Asilamu angawachitire zimene amawachitira anthu 
osakhulupirira monga kuwathira nkhondo akaputidwa. 



Surat 58. Al-Mujadilah Juzu 28 I 1194 I 1 A * >» ©A tai£i 5 j^-. 



17. Chuma chawo, ngakhale 
ana awo, Sizidzawathandiza konse 
ku chilango Cha Mulungu iwowo 
ndi Anthu a ku moto m'menemo 
Iwo adzakhala muyaya. 

18. (Alikumbukire) tsiku limene 
Mulungu Adzawaukitsa (ku imfa) 
onse, adzayamba Kulumbira kwa 
lye (zabodza) monga Akulumbira 
(zabodza) kwa inu. Akuganiza kuti 
apezapo kanthu (Pakulumbira 
kwawo). Dziwani, Ndithudi, iwo 
ndi abodza. 

19. Satana wawapambana ndipo 
Wawaiwalitsa kukumbukira 
Mulungu. Iwowa ndiachipani cha 
satana. Dziwani Kuti chipani cha 
satana nchotayika, (Choonongeka). 

20. Ndithudi, amene. 
akutsutsana ndi Mulungu ndi 
Mthenga Wake. Iwowo Adzakhala 
m'gulu la onyozeka. 

21. Mulungu adalamula (kuti): 
"Ndipambana Ine ndi Aneneri 
Anga." Ndithu, Mulungu 
ndiwanyonga zokwana 
Wopambana; (sapambanidwa ndi 
Aliyense). 

22. Supeza anthu okhulupirira 
mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza 
akukonda Amene akuda Mulungu 
ndi Mthenga Wake, ngakhale 
atakhala atate awo, ana Awo abale 
awo ndi akumtundu wawo; Kwa 












Surat 58. Al-Mujadilah Juzu 28 



1195 



tAt>! 



OA ibl£l $jj*i 



iwo (Mulungu) wazika 
Chikhulupiriro (champhamvu) 
m'mitima Mwawo, ndipo 
wawalimbikitsa ndi Mphamvu 
zochokera kwa lye. Ndipo 
Adzawalowetsa m'minda yomwe 
pansi Pake pakuyenda mitsinje; 
adzakhala M'menemo muyaya. 
Mulungu Adzakondwera nawo 
ndipo (iwonso) Adzakondwera 
Naye. Iwowa ndi chipani Cha 
Mulungu. Dziwani kuti Chipani 
cha Mulungu ndichopambana. 1 






1 M'ndime imeneyi Chauta akunenetsa kuti: "Amene akukhulupirira mwa 
Mulungu ndi Tsiku lomaliza, asapalane ubwenzi ndi munthu wodana ndi 
Mulungu ndi Mthenga Wake ngakhale wodana ndi Chautayo atakhala bambo 
wake, mwana wake ndi wina aliyense; apatukane nawo ndithu; chifukwa 
kupanda kutero akusonyeza kufooka kwa chikhulupiriro. Mtumiki (SAW) adati: 
"Munthu adzakhala ndi amene amamkonda pa tsiku Lachiweruzo." 



Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 



1196 



YA*j*-i o^yj-lojj^ 




Surayi yayamba ndi kufotokoza kuti zonse zakumwamba ndi 
zapansi pano zikulemekeza Chauta ndi kumuyeretsa ku mbiri 
zosayenerana ndi ulemerero Wake, ndi kuti lye ndiwopambana 
ndipo sapambanidwa; Wanzeru zakuya pa zochita Zake zonse. 

Zina mwazisonyezo za mphamvu Zake ndi nzeru Zake 
zakuya, yafotokoza surayi pa kulangidwa kwa Bani Nadhiri 
amene adali Ayuda aku Madina. Iwowa adagwirizana ndi 
Mneneri kukhalirana mwamtendere. Koma pamene Asilamu 
adagonja pankhondo ya Uhud, Bani Nadhiri adaswa panganolo 
ndi kugwirizana ndi Akuraishi kumthira nkhondo Mneneri 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) ndipo Mtumiki 
Muhammad(SAW) pamodzi ndi gulu lake adawazinga ayudawo 
m'malinga awo omwe anaganizira kuti angawateteze koma 
malingawo sadawateteze, ndipo Mneneri (madalitso ndi 
mtendere zikhale naye) adawasamutsa ku Madina. 

Kenako surayi yafotokoza za kagawidwe ka chuma cha Fayi- 
i. Fayi-i ndichuma chimene asiya adani popanda kubuka 
nkhondo kapena kuthamangitsa akavalo. Ndipo yafotokoza kuti 
chumacho ncha Mulungu, Mneneri, achibale a Mneneri, ana a 
masiye, masikini, munthu wa paulendo ndi osauka amene 
adasamuka ndi kusiya nyumba ndi chuma chawo. 

Surayi yafotokozanso za Ansari ndi ulemerero wawo; ndi 
kuti amatsogoza zofuna za abale awo owasamukira kuposa 
zofuna zawo. Ndipo yalongosolanso makhalidwe ena a anthu 
achinyengo amene amangosonyeza Chisilamu chawo ndi 
pakamwa pokha. 

Surayi yamaliza ndi kuchenjeza Asilamu kuti akhale oopa 
Mulungu ndi kukonzekera zanthawi yakutsogolo. 
Ikuwalangizanso kuti Qur'an ndi Buku la Mawu okoka mtima 
limene lidavumbulutsidwa ndi Mulungu, Mwini maina abwino; 
palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma lye basi. 



Surat 59. AI-Hashr Juzu 28 



1197 U^i 



o ^ j2±\ Sj^ 



Surat Al-HashrLIX 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Zonse zam'mwamba ndi 
zapansi Zimalemekeza Mulungu 
(ndi Kumuyeretsa ku khalidwe 
losayenera ndi Ulemerero Wake). 
Ndipo lye Ngopambana, 
(Salephera kanthu) Ngwaluntha 
(M'kakonzedwe Kake ndi 
m'zochita Zake). 

2. lye ndi Amene adatulutsa 
osakhulupirira Ena mwa anthu a 
Mabuku m'nyumba Zawo 
mkusamusidwa koyamba (Pa 
chilumba cha (Arabu). 
Simunkaganizira kuti angatuluke 
(M'nyumba zawozo). Ndipo iwo 
Amaganiza kuti malinga awo 
awateteza Kwa Mulungu. Koma 
Mulungu adawalanga kupyolera 
mmene Samayembekezera, ndipo 
adathira Mantha oopsa m'mitima 
mwawo (Potumiza Mtumiki Wake 
kwa iwo), Adagumula nyumba 
zawo ndi manja Awo ndi manja a 
okhulupirira. Lingalirani 
(zimenezi) E, inu eni nzeru! 1 



m 






Q^lt^l^ 



J& 



,7*v 









!T- 



1 Aya imeneyi ikulongosola nkhani ya kusamutsidwa kwa Ayuda otchedwa 
Bani Nadhiri mu mzinda wa Madina. Ayuda adasamutsidwa mumzinda wa 
Madina chifukwa cha kuswa mapangano okhalirana 
mwamtendere ndi Asilamu. 



Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 



1198 I 1A*>i 



o^ jJi^-l 5jj-- 



3. Ndipo kukadapanda kuti 
Mulungu Adawalembera 
(pachiyambi) kusamuka 
(M'nyumba zawo), akadawalanga 
Padziko pompano; koma chilango 
cha Moto chili pa iwo tsiku 
lomaliza. 

4, Zimenezo nchifiikwa chakuti 
iwo Adada Mulungu ndi Mthenga 
Wake,(Chidani chopyola muyeso); 
ndipo amene Akuda Mulungu 
(sangapulumuke ku Chilango 
Chake). Ndithu, Mulungu 
Ndiwolanga mwaukali. 

5. Sim'dadule mtengo uliwonse 
wa zipatso Za kanjedza, (inu 
Asilamu), kapena Kuusiya uli 
chiimire ndi thunthu lake koma 
Nchifuniro cha Mulungu ndi kuti 
Awayalutse otulukam'malamulo 
Ake. 1 

6, Ndipo chuma chimene 
wapereka Mulungu kwa Mtumiki 
Wake Chochokera kwa iwo (Bani 
Nadhiri), Chimenecho inu 
simudathamangitse Mahachi 
kapena ngamira (pakuchipeza) 
Koma Mulungu amapereka 
mphamvu Kwa aneneri Ake 















(Ndime 5-7) Ndime zimenezi zikufotokoza za kagawidwe ka chuma 
chosiyidwa ndi adani pankhondo.Chumacho sichongogawira amene amachita 
nkhondo okha ayi. Kapena kugawana akulu-akulu okha monga momwe 
amachitira ena omwe sali Asilamu pa nkhondo zawo. Chifukwa kutero ndiye 
kuti chumacho chizingozungulira pakati pa anthu olemera okhaokha ndi 
bwino. Chisilamu chikulamula kuti chuma choterechi chigawidwe kwa onse 
kuti umphawi uwachokere onse. 



Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 



1199 



YAs-jJrl 



O^ j£j-\ djj-»» 



zogonjetsera amene 
Wamfiina.Ndipo Mulungu ali ndi 
Mphamvu (pa) chilichonse. 

7. Chuma chimene Mulungu 
wachipereka Kwa Mneneri Wake 
cha anthu am'midzi (Yapafupi ndi 
mzinda wa Madina) Chimenecho 
ncha Mulungu, ndi Mneneri, ndi 
abale a Mneneri ndi Amasiye, ndi 
masikini, ndiponso Apaulendo; 
kuti chisakhale Chongozungulira 
pakati pa olemera okha Mwa inu. 
Ndipo chimene wakupatsani 
Mtumiki, chilandireni; ndipo 
chimene Wakuletsani chisiyeni. 
Muopeni Mulungu (potsatira 
malamulo Ake). Ndithu,Mulungu 
Ngwaukali polanga. 

8. Chiperekedwe kwa osauka 
osamuka omwe Adatulutsidwa 
m'nyumba zawo Ndi (kusiya) 
chuma chawo chifukwa Chofuna 
zabwino za Mulungu ndi Chikondi 
(Chake) ndi kupulumutsa 
Chipembedzo cha Mulungu ndi 
Mthenga Wake (potumikira matupi 
awo Ndi chuma chawo); Iwowa 
ndi (Asilamu) oona. 

9. Koma amene adakhala kale 
mumzinda Uwu (wa Madina) ndi 
kukhulupirira Akukonda amene 
adasamukira kwa iwo. Ndipo 
sakupeza vuto m'mitima mwawo 
Pazimene anzawo apatsidwa, 
ndipo Akutsogoza zofuna za 















*&"' 



i<i) 



Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 



1200 tA*>i 



^ j-*^"l *JJ"*' 



anzawo pazawo, Ngakhale iwo 
akuzifunitsitsa. Amene 
Atetezedwa (ndi Mulungu) 
kuumbombo Wa mitima yawo, 
amenewo ndiwo Opambana. 

10. Ndipo (okhulupirira) amene 
adadza Pambuyo (pa Amuhajirina 
ndi Ansari) Akunena kuti: "Mbuye 
wathu Tikhululukireni ndi anzathu 
amene Adatitsogolera pa 
chikhulupiriro, ndipo Musaike 

m' mitima m wathu njiru ndi 
Chidani kwa amene 
adakhulupirira. O, Mbuye wathu! 
Inu ndinu Wodekha Wachisoni." 

11. Kodi wawaona achinyengo! 
Amene akunena kwa Anzawo 
amene sadakhulupirire pakati Pa 
anthu a Mabuku: "Ndithu, Ngati 
(mukakamizidwa) kutuluka mu 
Mzinda wa Madina, tidzatuluka 
nanu Pamodzi ndipo sitingamvere 
aliyense za Inu mpaka muyaya; 
ngati Mutamenyedwa nkhondo 
(ndi Asilamu) 

Tidzakuthandizani.Koma Mulungu 
Akuikira umboni kuti iwo 
Ndionama (pazimene alonjeza). 

12. Koma akapirikitsidwa, 
sangatuluke nawo Limodzi; ngati 
atamenyedwa, Sangawathandize 
ndipo ngati Atawathandiza 
atembenuza Misana (kuthawa) 
Kenako sapulumutsidwa. 


















*-} 



Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 



1201 tA*>i 



o S j-iJ-l o j>*» 



13. Ndithu, inu (Asilamu) 
mukuopedwa Kwambiri m'mitima 
mwao kuposa mmene 
Akumuopera Mulungu. Zimenezo 
Nchifukwa chakuti iwo ndi anthu 
Osazindikira (chilichonse). 

14. (Ayuda) sangamenyane ndi 
inu ali pa Gulu kupatula m'midzi 
yotetezedwa Ndi malinga, kapena 
kuseri kwa zipupa. Nkhondo yawo 
pakati pawo njaukali; 
Ungawaganizire kuti ali pamodzi 
Pom we mitima yawo njosiyana; 
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo 
Ndianthu opandanzeru. 

15. Fanizo (la Ayuda a Banu 
Nadhiri) lili Ngati (amene 
adatsutsa mwa Ayuda A Kainuka) 
amene awatsogolera (Kupeza 
mavuto) posachedwapa, Adalawa 
chilango (padziko lapansi) Cha 
zochita zawo (ndi kuswa 
mapangano). Ndipo iwo 
adzalandira chilango (china) 
Chowawa kwambiri, (pa tsiku 
lachiweruzo) 

16. Fanizo la achinyengo 
(Amunafikuna Pakuwanyenga 
Banu Nadhiri kuti Amupandukire 
Mneneri wa Mulungu) Lili ngati 
satana (ponyenga munthu Kusiya 
chikhulupiriro). Adati kwa lye: 
"Mkane (Mulungu)." Ndipo 
pamene Adamkana, (satana) adati: 
"Ine sindili Ndi iwe; ndithu, ine 















Siirat 59. AI-Hashr Juzu 28 



1202 



YA*>! 



o H jJiJ-l 0jj-»» 



ndikuopa Mulungu, Mbuye wa 
zolengedwa." 

17. Choncho mapeto a onse 
awiriwo, Kudali kukalowa ku 
moto ndi kukhala M'menemo 
muyaya. Iyi ndiyo Mphoto ya 
anthu onyenga (ochenjerera 
Anzawo). 

18. E, inu amene 
mwakhulupirira! Muopeni 
Mulungu (potsatira malamulo Ake 
ndi Kusiya zimene waletsa) ndipo 
alingalire Munthu aliyense 
zamawa zimene Watsogoza 
muopeni Mulungu ndithu 
Mulungu, Ngodziwa zimene 
mukuchita (Ndipo adzakulipirani 
pa zimenezo). 

19. Musakhale, (inu 
okhulupirira) monga Amene 
aiwala zoyenera kuchitira 
Mulungu; (naye Mulungu) 
wawaiwalitsa Mitima yawo 
(powachotsera kuzindikira Zimene 
zingawathandize). Amene wa 
Ndiwo olakwa kwakukulu (otuluka 
Ku chilamulo cha Mulungu). 

20. Sangafanane anthu a ku 
moto, (Olangidwa), ndi anthu a ku 
Jannah, (Opeza mtendere). Anthu 
aku Jannah Ndiwo opambana. 

21. Chikhalakuti 
tidaivumbulutsa Qur'an iyi 
Pamwamba pa phiri, ukadaliona 


















Surat 59. Al-Hashr Juzu 28 I 1203 1 T A *>» 



OS j£±-\ Ojj-- 



phirilo Lili lodzichepetsa ndi 
kung'ambika Chifukwa choopa 
Mulungu. Awa ndi Mafanizo 
omwe tikuwapereka kwa anthu 
Kuti aganizire. 

22. lye ndi Mulungu, Amene 
palibenso Wina wopembedzedwa 
mwachoonadi Koma lye, Wodziwa 
zamseri ndi Zooneka. lye 
Ngwachifundo chambiri Ndiponso 
Ngwachisoni. 

23. lye ndi Mulungu, Amene 
palibenso Wina wopembedzedwa 
mwachoonadi Koma lye, Mwini 
chilichonse, Woyera, Mwini 
mtendere, wotsimikizira (aneneri 
Ake mphamvu yochitira 
zozizwitswa,) Msungi wa 
chilichonse (yemwe akuona 
Zochita za akapolo Ake;) 
Wamphamvu Zopambana, 
Mgonjetsi Wotukuka Muulemerero; 
Wamkulukulu.Wapatukana (dzina 
Mulungu kuzimene 
Akumuphatikiza nazo. 

24. lye ndi Mulungu; Mlengi 
wa (zinthu, Palibe chomfanizira); 
Muumbi wa Chilichonse. Mkonzi 
wa maonekedwe A zinthu, Ake ndi 
maina abwino, zonse Za kumwamba 
ndi pansi Zikumlemekeza lye ndi 
kumyeretsa Kumakhalidwe 
osayenerana ndi Ulemerero 
Wake.Iye wopambana Ndiponso 
Wanzeru zakuya. 















Surat 60. Al-Mumtabanah Juzu 28 



1204 



Y A tji-1 *\ ♦ &?CLtS\ 3jJ-» 




Surayi yayamba ndi kuwaletsa Asilamu kugwirizana ndi 
Amshirikina, amene ndi adani a Mulungu ndiponso adani awo 
pachifukwa cha kumkana Mulungu ndi kumsamutsa Mthenga 
wa Chauta mu mzinda wa Makka. Ndipo surayi yaloza chidani 
chimene chili m'mitima mwawo pa Asilamu chofuna 
kuwamaliza onse ngati angathe kutero. 

Yalongosolanso chitsanzo chabwino cha Ibrahim ndi amene 
adali nawo pamodzi, pakupatukana kwawo ndi Amushirikina 
ndi zimene amazipembedza kusiya Mulungu. Ndipo adalengeza 
chidanicho ndi iwo pokhapokha atamkhulupirira Mulungu 
mmodzi. 

Yalongosolanso za amene Asilamu angathe kugwirizana 
nawo mwa anthu azipembedzo zina ndi kukhalirana nawo 
mwamtendere; ndi amene nkosayenera kugwirizana nawo. Kwa 
amene sakutiputa ndipo sakuthandiza adani athu potichitira 
mtopola, tichite nawo chilungamo ndi kukhala nawo 
mwaubwino. Koma amene akutimenya pa chipembedzo ndi 
kuthandiza adani kutitulutsa m'nyumba zathu, iwo wo ndiomwe 
Chauta watiletsa kugwirizana nawo ndi kuwachitira zabwino. 

Kenaka yalongosola malamulo kwa Asilamu achikazi omwe 
asamukira ku Chisilamu ndi kusiya amuna awo Amushirikina. 
Ndiponso malamulo kwa akazi aopembedza mafano amene 
asamuka kusiya amuna awo Achisilamu kudziko la Shiriki 
(lopembedza mafano). Ndipo yatsatizanso kulongosola za 
lonjezo la akazi amene amalowa Chisilamu pazimene 
amamlonjeza Mneneri wa Mulungu (madalitso ndi mtendere 
zikhale naye). 

Surayi yamaliza ndi kuletsa kugwirizana ndi adani amene 
Mulungu wawakwiira. 



Surat 60. Al-Mumtahanah Juzu 28 



1205 ™ *>< 



*l ♦ <U^cull dja-j 



Surat Al-Mumtahanah LX 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musawachite 
adani Anga Ndi adani anu kukhala 
athandizi anu ndi Kumawauza 
(nkhani zanu) mwa chikondi, 
Pomwe iwo sanakhulupirire 
choonadi Chimene chakudzerani. 
Mneneri Wake, Adamtulutsa 
Mtumiki ndi inu nomwe 
(M'nyumba zanu) chifukwa 
chakuti Mumakhulupirira 
Mulungu, Mbuye wanu, (Palibe 
cholakwa chilichonse chimene 
Mudawachitira,) ngati mwatuluka 
Kukachita Jihad pa njira Yanga ndi 
Kufunafuna chikondi Changa; 
(musapalane Nawo ubwenzi) 
mukuwatumizira chinsinsi. (Chanu 
cha nkhondo) chifukwa cha 
Chikondi (chanu ndi iwo); 
(Musachitenso zimenezi) pomwe 
Ine Ndikudziwa zimene inu 
mukubisa ndi Zimenene 
mukuzisonyeza (poyera); Amene 
akuchita zimenezi mwa inu, Ndiye 
kuti wataya njira yoongoka. 1 



O^ly^ll^ 






1 Inu Asilamu amene mwakhulupirira mwa Mulungu ndi Mthenga Wake(SAW) 
musawachite makafiri amene ndi adani anga ndiponso adani anu kukhala 
okondedwa anu ndi abwenzi anu. Chisonyezo cha chikhulupiriro kwa Msilamu 
ndiko kuwada adani a Mulungu, osati kuwakonda ndi kupalana nawo ubwenzi. 



Su rat 60. Al-Mumtahanah Juzu 28 1 206 TA ^jA-i 



"V • <U?i£felt djj~*> 



2. Akakumana nanu 
(pankhondo) akukhala Adani anu 
ndipo akukutambasulirani Manja 
ndi malirime awo moipa 
(Pokumenyani ndi 
kukutukwanani); ndipo 
Akulakalaka mukadakhala 
Osakhulupirira (kuti mufanane 
nawo). 

3. Abale anu ngakhale ana anu 
Sadzakuthandizani tsiku la Kiyama 
(Mulungu) adzaweruza (pakati 
panu), Ndipo Mulungu akuona 
Zimene mukuchita. 

4. Ndithu, inu muli ndi 
chitsanzo chabwino Cha (mtumiki) 
Ibrahima ndi amene Adali naye 
pamene adawauza anzawo 
(Osakhulupirira kuti): "Ndithu, ife 
Tapatukana nanu pamodzi ndi 
milungu Yanu imene 
mukuipembedza kusiya Mulungu; 
takukanani, ndipo chidani ndi 
Kusakondana zaonekera poyera 
pakati Pa inu ndi ife mpaka 
muyaya, kufikira, Mutakhulupirira 
mwa Mulungu mmodzi (Inunso 
chitani chimodzimodzi, muwakane 
Abale anu amene ali akafiri), 
kupatula Mawu a Ibrahima pamene 
adamuuza tate Wake (kuti): 
"Ndithu, ndikupempherani 
Chikhululuko. Palibe chimene 
Ndingakutetezereni nacho kwa 
Mulungu (Ngati mutamuphatikiza 



mm 



^&^mmm 






Surat 60. Al-Mumtahanah Juzu 28 



1207 TA*>1 



1 ♦ 4^cull 



°J>" 



Mulungu ndi zina". Mawu 
amenewo musatsatire koma 
Pempherani motere:) "O, Mbuye 
wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo 
kwa Inu Tatembenukira ndiponso 
Kobwerera nkwa inu." 1 

5. O, Ambuye athu! Musatichite 
kukhala Mayeso kwa amene 
sadakhulupirire, Tikhululukireni 
Mbuye wathu! Ndithu Inu, Ndinu 
Amphamvu zopambana Ndiponso 
Anzeru zakuya. 

6. Ndithu muli nacho inu kwa 
iwo (Ibrahima Ndi omsatira) 
chisanzo chabwino kwa Amene 
akuyembekezera kukumana ndi 
Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo 
Amene anyozere ndithu, Mulungu 
Ngolemera (ndipo) 
Ngotamandidwa. 

7. Mwina Mulungu angaike 
chikondi Pakati panu ndi ena mwa 
amene Mumawada (poiongolera 
mitima yawo Kukhulupirira mwa 
Mulungu), Mulungu Ngokhoza 
chilichonse Ndiponso Mulungu 
Ngokhululuka; Ngwachisoni. 

8. Mulungu sakukuletsani 
kuwachitira Zabwino ndi 









&?•"■'-" 









a^%&\^\^^ 



1 Apa akutiuza kuti titsanzire zimene adachita tate wa Shariya amene ndi 
Ibrahima pamodzi ndi omtsatira ake pamene adadzipatula kwa makolo awo 
ndi abale awo omwe adali m'chipembedzo chonama.Msilamu amkonde 
Mulungu kuposa tate wake, ana ake, mkazi wake, chuma chake ndi thupi lake 
limene. Atsogoze zofuna za Mulungu asanachite china chilichonse. Akatero 
akhala kuti wakhulupirira Mulungu mwachoonadi. 



Surat 60. Al-Mumtahanah Juzu 28 



1208 



YAc>» 



1, * 4a * &»ll 3jJ-*» 



chilungamo amene 
Sadakumenyeni ndi kukutulutsani 
M'nyumba zanu chifukwa cha 
Chipembedzo.Ndithu, Mulungu 
Akukonda Achilungamo. 1 

9. Mulungu akukuletsani 
kugwirizana Nawo amene 
adakumenyani chifukwa Cha 
chipembedzo ndi kukutulutsani 
M'nyumba zanu, ndi amene 
adathandiza Kukutulutsani. Amene 
ati agwirizane Nawo Iwowo ndiwo 
Achinyengo. 

10. E, inu amene 
mwakhulupirira! Akakudzerani 
Asilamu achikazi Osamuka, 
ayeseni mayeso (kuti Mudziwe 
chikhulupiriro chawo); Mulungu 
ali wodziwa kwambiri za 
Chikhulupiriro chawo; ngati 
Mutawadziwa kuti ndiokhulupirira 
Musawabwezere kwa 
osakhulupirira. Akaziwo saloledwa 
kukwatiwa ndi Osakhulupirira, 
iwonso saloledwa Kuwakwatira. 
Abwezereni chiwongo Chimene 
adapereka amuna 
Osakhulupirirawo. Ndipo palibe 
tchimo Kwa inu kuwakwatira, 
(ngakhale adasiya Amuna awo 
achikafiri (ku Makka) Ngati 
muwapatsa chiwongo chawo. 



9> >l'Z 9 '\ 9 t\' 'vrHfiZj'i' >ll 



»&4' 



* % 









© 



1 Mulungu sakutiletsa kuwachitira zabwino anthu amene sali Asilamu, mmalo 
mwake akutilamula kuti tiwachitire zabwino ngati alibe upandu uliwonse ndi 
Asilamu. 



Surat 60. Al-Mumtahanah Juzu 28 



1209 TA*>i 



*\ • 4,'^cull 5jJ-»» 



Musakangamire maukwati ndi 
akazi Achikafiri (osakhulupirira 
amene Adatsalira ku Makka). 
Itanitsani Zimene mudapereka kwa 
akazi anu (Achikafiriwo), naonso 
Akafiri aitanitse Zimene adapereka 
(kwa akazi awo Akalowa 
m'Chisilamu). Limeneli ndi 
Lamulo la Mulungu limene 
Akulamula pakati panu. Mulungu 
Ndiwodziwa kwambiri ndiponso 
Ngwanzeru poika malamulo. 

11. Ndipo ngati mmodzi mwa 
akazi anu Atakuthawani kupita 
kwa Akafiri, Ndipo 
(mwadzidzidzi) mwakachita 
Nkhondo (ndi kupeza chuma 
chosiya Adani anu), apatseni 
amene awathawa Akazi awo 
chofanana ndi chimene Adapereka 
(pokwatira). Ndipo Muopeni 
Mulungu amene inu 
mukumkhulupirira. 

12. E, iwe Mtumiki! 
Akakudzera akazi Okhulupirira 
kudzakulonjeza kuti Samphatikiza 
Mulungu ndi chilichonse Ndi kuti 
saziba,sazichita chiwerewere, 
Sazipha ana awo ndi kuti sazinena 
Bodza lamkunkhuniza, lomwe 
akulipeka Pakati pa manja awo ndi 
miyendo yawo (Pompachika 
mwana kwa wina amene Sali tate 
wake), ndi kutinso Sadzakunyoza 
pachinthu chabwino (Chimene 






&''JA1 






Surat 60. AI-Mumtahanah Juzu 28 



1210 



tA *>i 



*\ ♦ <U*tioil Oj^mi 



ukuwaitanira), landira Lonjezo 
lawolo, ndipo apemphere 
Chikhululuko kwa Mulungu. 
Ndithu Mulungu 
NgokhululukaKwambiri, 
Ngwachisoni. 

13. E, inu amene 
mwakhulupirira! Musagwirizane 
ndi anthu amene Mulungu 
wawakwiyira ndipo ataya Mtima 
wopeza mphoto tsiku lomaliza 
(Chifukwa cha machimo awo 
ochuluka) Monga momwe atayira 
mtima akafiri Za kuuka kwa 
amene ali m'manda. 







Surat 61. As-Saff Juzu 28 



1211 



Ut>t 



*\ \ uuaJl 5jj^ 




Surayi yayamba ndi kufotokoza kuti zakumwamba ndi za 
m'dziko lapansi zikulemekeza Mulungu ndi kumyeretsa ku 
Makhalidwe osayenerana ndi ulemerero Wake. Ndipo yapitiriza 
kunena kuti nkosayenera kwa okhulupirira kuyankhula zimene 
sakuchita ndi kuti Chauta amakonda kuti iwo azikhala dzanja 
limodzi kwa adani awo. Kenako yafotokoza za kupandukira 
choonadi kwa ana a israeli kupyolera mmalireme a Mithenga 
iwiri yolemekezeka: Musa ndi Isa, ndi kuti iwo amayesetsa 
kuzimitsa kuunika kwa Mulungu, koma Chauta amakwaniritsa 
kuunika Kwake. 

M' surayi muli lonjezo la Mulungu lakuti atukula 
chipembedzo Chake cha Chisilamu kuti chikhale pamwamba pa 
zipembedzo zina ngakhale anthu ophatikiza Chauta ndi mafano 
chikuwaipira chipembedzochi. 

Pomalizira surayi yalimbikitsa Asilamu kuchita (Jihad) 
panjira ya Mulungu pochita ndi chuma ndi matupi awo. Ndipo 
ochita (Jihad) yawalonjeza kuti adzakhululukidwa machimo 
awo ndi kukalowa ku Jannah. Okhulupirira yawalimbikitsanso 
kuti akhale athangati pa chipembedzo cha Mulungu monga 
momwe adalili ophunzira a Isa mwana wa Mariam. Ndipo 
Chauta adzalimbikitsa okhulupirira ndi chithandizo Chake lye 
Ngopambana chilichonse, Mwini nzeru zokwanira. 




Surat 61. As-Saff Juzu 28 



1212 *A*>i 



1 1 Jl*}\ Ijf* 



Surat As-SaffLXI 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Zonse zakumwamba ndi 
zapansi Zimalemekeza Mulungu 
(ndi Kumyeretsa kumakhalidwe 
osayenera Ndi ulemerero Wake). 
Ndipo lye yekha Ngopambana pa 
chilichonse; Wanzeru Zakuya. 

2. E, inu amene 
mwakhulupirira! Bwanji 
mukunena Zimene simuchita? 1 

3. Mulungu amakuda Zedi 
kunena zinthu Zimene simuchita. 

4. Ndithu, Mulungu akukonda 
amene Akumenya nkhondo Panjira 
Yake (yofalitsa Chipembedzo 
Chake), ali pamzere (Umodzi) uku 
ali monga chomanga, Chomangika 
mwamphamvu. 2 

5. Ndipo (kumbuka iwe 
Mneneri{SAW}) Pamene Musa 
adanena kwa anthu ake kuti: 
"Ndichifukwa ninji 
mukundivutitsa ine mukudziwa 



v*. 



■ 



Q^JHt^jll^ 



■& 



osssa 



uSSS^SsWfi 



©< 









(Ndime 2-3) Khalidwe la munthu limene limakwiyitsa Mulungu kwambiri 
ndiko kunena zokoma chikhalirecho zochita zili zoipa. Amawanyenga anthu 
ndi mawu otsekemera koma zochita zake ndizachinyengo zokhazokha. 
Munthu wa makhalidwe otere, malipiro ake ndi kulowa ku nthukutira yamoto. 
Choncho zochita zanu zifanane ndi zimene mukuyankhula. Apeweni 
makhalidwe achiphamaso. 

2 Mulungu akufuna kuti Asilamu akhale dzanja limodzi pofalitsa Chisilamu, 
agwire ntchito yokomera gulu lonse mothangatana. 



Surat 61. As-Saff Juzu 28 



1213 



ta ^jA-i 



*V ^ uLaJi «jj-» 



kuti ine ndine Mtumiki wa 
Mulungu kwa inu?" Ndipo pamene 
Adapitiriza kupandukira choonadi, 
Mulungu adaipinda mitima Yawo 
(kuti isalandire chiongoko); 
Mulungu saongola anthu otuluka 
M'chilamulo Chake. 

6. Ndiponso (kumbuka) pamene 
adanena (Mtumiki) Isa mwana wa 
Mariam, Kuti: "E inu ana a 
Israeli INdithu ine Ndine Mtumiki 
wa Mulungu kwa inu, Amene 
ndikuchitira umboni zimene 
Zidadza patsogolo panga za buku 
la Chipangano chakale (Torah) 
ndipo Ndikuuzani nkhani yabwino 
ya mthenga Amene adzadze 
pambuyo panga, dzina lake 
Ahamad (Muhammad{SAW})'\ 
Koma Pamene adawadzera 
(Mtumiki Wolonjedzedwayo) ndi 
zisonyezo Zowonekera poyera 
(kuti iye ndi Mtumiki wa 
Mulungu). Adati: "AwaNdi 
matsenga owonekera". 

7. Kodi ndani oipitsitsa kuposa 
yemwe Wapekera Mulungu bodza, 
pomwe iye Akuitanidwira ku 
Chisilamu (Chipembedzo choona 
ndi chabwino)? Ndipo Mulungu 
saongola anthu Achinyengo. 

8. Akufuna kuti azimitse 
dangalira la Mulungu ndi 
pakamwa pawo ndipo Mulungu 
Ngokwaniritsa dangalira Lake 



®&J\2$\ 



>'t* f "i\i \>>' \*t'>' 1\'$A 






'9 






Surat 61. As-Saff Juzu 28 



1214 



TA «.j*-» 



*\ ) uLaJl Qjy 



Ngakhale ziwaipire 
osakhulupirira. 1 

9. lye ndi amene adatuma 
Mtumiki Wake 
(Muhammad{SAW}) ndi 
chiongoko Ndi chipembedzo 
choona, kuti achiike Pamwamba 
pa zipembedzo zonse, Ngakhala 
kuti ophatikiza Mulungu ndi 
Mafano zikuwaipira. 

10. E, inu amene 
mwakhulupirira! Kodi 
Ndikudziwitseni malonda amene 
Angakupulumutseni ku chilango 
Chowawa? 

11. Muzimkhulupirira Mulungu 
ndi Mtumiki Wake; ndipo 
muzichita Jihad pa njira ya 
Mulungu ndi chuma chanu, ndi 
matupi Anu. Zimenezo nzabwino 
kwa inu Ngati muli odziwa. 

12. Akukhululukirani machimo 
anu ndipo Akulowetsani m'minda 
momwe Mitsinje ikuyenda pansi 
pake, ndiponso (Adzakupatsani) 
mokhala mwabwino Ku minda 
yamuyaya. Kumeneko ndiko 
Kupambana kwakukulu. 

13. Ndizina zomwe 
mukuzifuna. Thandizo (Lonse) 
lichokera kwa Mulungu ndi 






*> 









'4 i 









1 (Ndime 8-9) Mulungu akulonjeza kuti Chisilamu chidzapambana zipembedzo 
zonse ngakhale osakhulupirira akuchithira nkhondo. 



Surat 61. As-Saff Juzu 28 



1215 tA*>» 



*\ \ Juph\ djj-*i 



Kugonjetsa kumene kuli pafupi; 
ndipo Auze nkhani yabwino 
Okhulupirira, 

14. E, inu amene 
mwakhulupirira! Khalani 
Othangata kufalitsa chipembedzo 
cha Mulungu (pamene Mtumiki 
akukuitanani Kuti mumthangate) 
monga momwe Adanenera Isa 
mwana wa Mariam Powauza 
otsatira ake: "Ndani 
Adzandithangata pa ntchito ya 
Mulungu (Yofalitsa chipembedzo 
Chake)? Otsatira ake adanena: "Ife 
ndife Othangata (kufalitsa 
chipembedzo cha) 
Mulungu."Choncho gulu Una la 
ana a Israeli lidakhululupirira, 
ndipo gulu Lina 
silidakhululupirire, tero 
Tidawapatsa mphamvu amene 
Adakhulupirira pa adani awo, 
ndipo Adali opambana. 



"if" -V T J> i5'-'r , " l ^fTli , " , f!' 



9 "L'S* ""i 




Surat 62. Al-Jumu'ah Juzu 28 



1216 



YA*>» 



*\ Y 4Jt*i*l djj-a 



SURAT AL-JUMU'AH LXII 





Surayi yayamba ndi kufotokoza kuti zonse za kumwamba ndi 
zapansi zikulemekeza Mulungu ndi kumpatula ku makhalidwe 
osayenerana ndi ulemerero Wake. Ndipo kenaka yatchula 
mtendere umene Chauta adaupereka kwa Aarabu amene 
samadziwa kulemba ndi kuwerenga powatumizira Mneneri 
wochokera mwa iwo kuti awaphunzitse nzeru ndi kuwayeretsa. 

Ndithu, chimenechi ndichisomo cha Mulungu chomwe 
amachipereka kwa amene wamfuna. 

Kenako surayi yadzudzula Ayuda chifukwa cha kusiya 
kutsatira malamulo omwe adali m'chipangano chakale. Ndipo 
yatsutsa bodza lawo loti iwo okha ndiwo okondedwa ndi 
Chauta, osati mitundu ina. Ndiponso yawabetchera kuti ngati 
akunena zoona ailakelake imfa kuti akakumane ndi 
wokondedwa wawoyo. Koma sangathe kutero chifukwa cha 
machimo awo amene adawachita. 

Kenako yamaliza ndi kulamula Asilamu kuti achite changu 
kukapemphera swala ya jumu'a akamva kuitana; ndi kuti asiye 
malonda, ndipo swala ikatha, abalalikane padziko kunka 
nafunafuna zabwino za Mulungu. Ndiponso yawalangiza kuti 
malonda ndi masewero zisawachititse kukhala otanganidwa 
nazo ndi kusiya kumvera ulaliki wa tsiku limenelo. 




Surat 62. Al-Jumu'ah Juzu 28 



1217 



YA frjJUl 



% Y AjtJrl 3jj-» 



Sural Al-Jumu'ah LXI1 




M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Zonse zakumwamba ndi 
dziko lapansi Zikulemekeza 
Mulungu; Mfumu Woyera, 
Wamphamvu zopambana ndi 
nzeru Zakuya (ndi kumyeretsa ku 
makhalidwe Osayenerana ndi 
ulemerero Wake). 

2. lye ndiAmene adatumiza kwa 
Ummiyyina (Osadziwa kulemba 
ndi kuwerenga), Mtumiki 
wochokera mwa iwo kuti 
Awawerengere ndime Zake ndi 
kuti Awayeretse (ku uchimo ndi 
Kumakhalidwe oipa) ndi 
kuwaphunzitsa Qur'an ndi mawu 
anzeru (Amtumiki) ndithu kale 
adali Osokera kowonekera 
(Mtumiki {SAW} Asadadze kwa 
iwo). 1 



o^l^JMU- 









1 Arabu amatchedwa "Ummiyyuna" chifukwa chakuti samadziwa kulemba ndi 
kuwerenga. Kusadziwa kulemba ndi kuwerenga kudafala pakati pawo ndipo 
ngakhale Mtumiki amene samadziwa kulemba ndi kuwerenga chilichonse. 
M'ndime imeneyi, Mulungu akutiphunzitsa kuti adampereka Muhammad 
(madalitso ndi mtendere zikhale naye) kuti awaongolere anthu kunjira 
yoongoka. lyeyu adaperekedwa panyengo imene anthu adali ndi khumbo la 
Mneneri wa Mulungu kuti watsogolere ku njira yolungama pakuti pa nthawiyo 
zipembedzo zonse za Mulungu zidali zitaonongeka. Pachiyambi Arabu 
amatsatira chipembedzo cha Ibrahim. Kenako adasintha nkuyamba 
kupembedza mafano. Adayambitsa zinthu zambiri zosalolezedwa ndi Chauta. 
Ndipo nawonso anthu amabuku, Ayuda ndi Akhrisitu, adasintha zophunzitsa 
za mabuku awo. Choncho Mulungu adapereka Muhammad(SAW) ndi 
malamulo aakulu okwanira bwino. Mkati mwake mudali chilichonse chofunika 



Surat 62. Al-Jumu'ah Juzu 28 



1218 



YA*jA-l 



*\ V AjuJrl Ojj-*» 



3. Ndipo (adamtumizanso) kwa 
ena Mwa iwo, omwe sadakumane 
nawo, Ndipo lye (Mulungu) 
Ngopambana (Pa chinthu 
chilichonse ndi Wamphamvu 
Zoposa ndiponso) Wanzeru zakuya. 

4. Umenewo ndiwo ubwino wa 
Mulungu akuupereka kwa amene 
Wamfuna (mwa akapolo Ake); 
ndipo Mulungu yekha ndi Mwini 
Ubwino waukulu. 

5. Fanizo la (Ayuda) amene 
Adawasenzetsa Taurat 
(chipangano Chakale, 
pokakamizidwa kuti atsatire 
Zophunzitsa za bukulo, koma 
Osatsatira), ali ngati Bulu amene 
Akusenza mabuku akuluakulu 
anzeru, (Koma osathandizidwa 
nawo). Taonani kuipa fanizo la 
anthu amene Atsutsa zisonyezo za 
Mulungu. Ndipo Mulungu 
saongola anthu achinyengo. 1 

6. Nena: "E, inu Ayuda! Ngati 
Mwadziganizira kuti ndithu, ndinu 
Okondedwa a Mulungu kuposa 
(Mitundu ina ya) anthu, ilakelakeni 
Imfa (kuti mukalowe ku mtendere 
wa Mulungu) ngati mukunena zoona. 



ws^ffm^m 












m'moyo wa anthu pa nyengo zosiyanasiyana pa moyo wa padziko ndi wa pa 
tsiku lomaliza. Mulungu adampatsa zabwino zomwe sadampatseponso wina 
aliyense, woyamba ndi womaliza. 

1 Mulungu Wotukuka, akufanizira Ayuda amene amadziwa kuwerenga Taurat 
bwinobwino, koma zomwe akuwerengazo osazigwiritsa ntchito, ngati bulu 
wosenza mabuku akuluakulu popanda chopeza pomwe mabukuwo ali odzaza 
ndi zinthu zabwino zophunzitsa nzeru zabwino. 



Surat 62. Al-Jumu'ah Juzu 28 



1219 



TA*j*-l 



*\ t AjuJrl Ojj-» 












\ ^.'i-l'&dLjKjif 



l<oj>yy 



%$2ftZiP$ 






7. Ndipo sangailakelake 
Mpang'ono pomwe chifukwa cha 
(zoipa) Zimene manja awo 
atsogoza! Ndipo Mulungu 
akudziwa bwino za (anthu) 
Osalungama. 

8. Nena (kuti): "Ndithu, imfa 
imene Mukuithawa (palibe 
chipeneko) Ikumana nanu; kenako 
muzabwezedwa Kwa Wodziwa 
zobisika ndi zooneka; Ndipo 
adzakuuzani zimene mudali Kuchita. 

9. E, inu amene 
mwakhulupirira! Kukaitanidwa 
kuswala (mapemphero) Tsiku la 
Ijumaa, pitani Mwachangu 
kukamtamanda Mulungu, Ndipo 
siyani malonda; zimenezo 
(Mwalamulidwazo) mzabwino 
kwa Inu ngati mukudziwa. 1 

10. Tsono Swala ikatha, 
balalikanani padziko, Ndipo funani 
ubwino wa Mulungu; Ndipo 
mtamandeni Mulungu (ndi mitima 
Yanu, ndi malirime anu) kwambiri 
Kuti mupambane (padziko lapansi 
Ndi pa tsiku lomaliza). 



1 M'ndime imeneyi akutiphunzitsa kuti tikamva adhana (kuitana) tsiku la ljuma, 
tisiye chilichonse chimene tikuchita ndi kupita mwachangu kukapemphera 
pemphero la ljuma. Pempheroli ndilofunika kwa Msilamu aliyense makamaka 
amuna. 

Asilamu amasonkhana m'Misikiti ikuluikulu pa tsiku limeneli pa sabata 
iliyonse. Ndipo pa tsiku limeneli ndipomwe Mulungu adakwaniritsa zolenga 
zake zonse. Adamu adalengedwa pa tsikuli ndipo adalowetsedwa ku Jannah 
tsiku lomweli. Ndipo adatulutsidwa m'menemo pa tsiku la ljuma. Mtumiki 
adafotokozanso za kuti Kiyama idzadza tsiku la ljuma. 






©& 



'.>?[:£'< 



Surat 62. Al-Jumu'ah Juzu 28 1220 * * *>' 



1 1 4*uJH 5jj-- 



11. Ndipo akaona malonda 
kapena Masewero, akubalalika 
kunka ku Zimenezo ndi kukusiya 
uli chiimire (Ukuchita khutuba ndi 
anthu ochepa). Nena (kwa iwo): 
"Zimene zili kwa Mulungu 
nzabwino kwa inu kuposa 
Masewero ndi malonda. Ndipo 
Mulungu Ngwabwino kwambiri 
kuposa Opatsa onse. 







Surat 63. AI-Munafiqun Juzu 28 1 1221 I *A *>! n r *f*M ^ 




Surayi yasonkhanitsa makhalidwe a anthu achinyengo ndi 
kufotokoza za iwo kuti amaonetsera poyera chikhulupiriro 
chawo ndi malirime awo abodza. Ndipo yalongosola kuti iwo 
akuchiyesa chikhulupiriro chawo chonama kukhala chishango 
chawo chodzitchinjiriza nacho kuti asatchedwe kuti ndi akafiri 
(osakhulupirira). Kenaka yalongosolanso kuti iwo ndi eni 
matupi okongola; osalala kwa yemwe wawaona. Ndipo zonena 
zawo nzomveka bwino kwa yemwe wazimva. Koma ngakhale 
ali tero, iwo m'mitima mwawo mulibe chikhulupiriro ngakhale 
pang'ono. Ali ngati chikuni chimene chasamizidwa; mulibe 
moyo mwa iwo, wauzimu. 

Surayi yafotokozanso za iwo kuti amadzikweza Mtumiki 
akawaitana kuti awapemphere chikhululuko. Kenako yatsutsa 
bodza limene anthu achinyengo amanena kuti iwo 
ngolemekezeka ndipo Asilamu ngonyozeka. Ndipo pomaliza 
yalimbikitsa Asilamu kuti apereke chuma chawo panjira ya 
Mulungu mwachangu imfa isadampeze mmodzi wa iwo kuti 
asadandaule ndi kulakalaka kuti ndibwino akadaonjezeredwa 
nthawi ya moyo wake. Koma Mulungu sangauchedwetse mzimu 
nthawi ya imfa yake ikafika. 




Surat 63. Al-Munafiqun Juzu 28 1222 * A *>' 



■vro^uii Sjj-- 



Surat Al-Munafiqun LXIII 



"fc;^; $ȣ ;;Sp 



,, __ r^v— 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Akakudzera achinyengo 
akunena kuti: "Tikuikira umboni 
kuti iwe ndiwe Mtumiki wa 
Mulungu ndipo Mulungu 
Akudziwa kuti iwe ndiwe mtumiki 
Wake." Ndipo Mulungu akuikira 
Umboni kuti achinyengo ngabodza 
(Pa zomwe akunena). 

2. Kulumbira kwawo (kwa 
bodza) Akuchita kukhala 
Chotetezera (chuma chawo Ndi 
matupi awo). Ndipo atsekereza 
(Anthu kuyenda) panjira ya 
Mulungu Ndithu nzoipa zedi 
zimene amachita. 

3. Zimenezo nchifukwa chakuti 
Iwo Adakhulupirira 
(modzionetsera), Kenako adakana 
(mobisa). Choncho Mitima yawo 
idatsekedwa kotero kuti Iwo 
sangathe kuzindikira (chimene 
Chingawapulumutse Ku chilango 
cha Mulungu.) 

4. Ndipo ukawaona, 
akukondweretsa Matupi awo; 
ndipo akayankhula Umvetsera 
zoyankhula zawo (Chifiikwa 
chakuthwa kwa malirime Awo, 
pomwe mkati mwawo Nding'oma 



o^l<^3ll*iU. 









^^^m^^ 






a 



bi> 






Surat 63. Al-Munafiqun Juzu 28 



1223 



YA*>! 



nr o^duii 5jj**» 



yopanda kanthu); iwo ali Ngati 
matsinde a mitengo yomwe 
Yayadzamiritsidwa ku chipupa; 
(mwa Iwo mulibe moyo).Mkuwe 
uliwonse (Umene akuumva) 
akuganiza kuti Ukulinga 
iwo,(chifiikwa cha Kuzindikira 
chinyengo chawo); iwowa Ndi 
adani; chenjerani nawo. Mulungu 
Awatemberere!Mwanjira yanji 
Akuchotsedwa (kuchoonadi)! 

5. Kukanenedwa kwa iwo kuti: 
"Bwerani, Akupemphereni 
chikhululuko mthenga Wa 
Mulungu, akutembenuza mitu 
yawo (Monyoza ndi 
modzitukumula), ndipo Uwaona 
akunyoza uku akudzikweza 
(Osasatira langizo). 

6. Kwa iwowa nchimodzimodzi 
Kuwapemphera kwako 
chikhuluko, Kapena 
kusawapemphera. Mulungu 
sangawakhululukire (Chifukwa 
cha kuzama kwawo 
M'kusakhulupirira). Ndithu, 
Mulungu Saongola anthu otuluka 
m'chilamulo Chake. 

7. Amenewa ndiwo omwe 
akunena (kwa Ansari; (Asilamu 
aku Madina, kuti): "Musawapatse 
chuma (chanu) amene Ali ndi 
Mtumiki wa Mulungu kuti 
Abalalikane.'Tomwe nkhokwe 









"*i? 






Surat 63. Al-Munafiqun Juzu 28 



1224 



XA*>1 



nr o^sLii 9jj~> 



zonse (Zachuma) za kumwamba 
ndi dziko Lapansi zili m'manja 
mwa Mulungu (ndipo 
amachipereka kwa Amene 
wamfuna); koma achinyengo 
Sakuzindikira (zimenezo). 1 

8. Akunena kuti: "Ngati 
tibwerera ku Madina 
wolemekezeka adzatulutsa 
Wonyozeka m'menemo. " Pomwe 
Ulemerero ngwa Mulungu ndi 
Mthenga Wake ndi okhulupirira; 
koma Achinyengo sakudziwa 
(Zimenezo). 

9. E, inu amene 
mwakhulupirira! Chuma Chanu 
ngakhalenso ana anu 
Zisakutangwanitseni ndi kusiya 
Kukumbukira Mulungu (ndi 
kukwaniritsaZimene 
wakulamulani). Ndipo amene 
Achite zimenezo iwo ndi otaika. 

10. Perekani mwachangu 
(panjira ya Mulungu) zina mwa 









ofe 3<$&^%^&^j 



1 (Ndime 7-8) Chifukwa chomwe ndime izi zidavumbulutsidwira ndi kuti tsiku 
lina Mtumiki(SAW) pomwe adali ndi gulu lake la nkhondo, munthu wina wa 
m'madera am'midzi adakangana ndi Msilamu wa mumzinda wa Madina 
chifukwa cha madzi. Ndipo Mwarabu wa kumudzi uja adamenya Msilamu wa 
m'Madina ndi thabwa. Poona izi Msilamu wa ku Madina adapita kukasuma kwa 
mwana wa Ubayye amene adali Munafiki (wachinyengo). Ubayyeyo adamuuza 
wosumayo kuti: "Musamawapatse chakudya omwe ali ndi Muhammad kuti 
abalalikane, athawe njala ndi kumsiya yekha Muhammad(SAW)." Adatinso: 
"Tikabwerera ku mzinda wa Madina, wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka." 
Apa amatanthauza kuti wolemekezeka ndiye iye, ndipo wonyozeka ndi 
Mtumiki Muhammad (madalitso ndi mtendere zikhale naye). Ndipo Mulungu 
adamuyankha ponena kuti: "Kulemekezeka ndi kwa Mulungu ndi Mthenga 
wake ndi okhulupirira; koma anthu achinyengo sakudziwa zimenezi." 



Surat 63. Al-Munafiqun Juzu 28 1225 I *A *>» 



M" o^flduii Sjj-- 



zomwe Takupatsani, isanamfikire 
mmodzi Wainu imfa 
(mwadzidzidzi) ndi Kuyamba 
kunena (modandaula), "Mbuye 
wanga! Bwanji Osandichedwetsa 
nthawi pang'ono Kuti 
ndikhulupirire (ndi kuti Ndikonze 
zina zimene Sindinazikwaniritse) 
ndi kutinso Ndikhale mwa anthu 
anu abwino." 

11. Ndipo Mulungu 
sauchedwetsa Mzimu (ngakhale 
ndi mphindi Imodzi) ukaidzera 
nthawi yake ya Imfa; ndipo 
Mulungu Ngodziwa Zonse zimene 
mukuchita, (ndipo Adzakulipirani 
pa zimenezo). 










Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 1226 TA tjA-t M ^ifcli Sj^ 




Surayi yayamba ndi kufotokoza kuti zonse zakumwamba ndi 
zam'dziko lapansi zikumpatula Mulungu ku zinthu zosayenera 
ndi ulemerero Wake, ndi kuti lye ndi mwini ufumu ndiponso 
Mwini kuyamikidwa. Ndi kutinso lye ali ndi mphamvu pa 
chilichonse. 

Kenako yasonyeza zisonyezo za kukwanira kwa nzeru Zake 
ndi mphamvu Zake. Ndipo yafotokoza za amene adamkana kale 
ndi kunyoza aneneri a Mbuye wawo, ndi m'mene adalawira 
chilango pa machitidwe awo oipa. 

Zimenezo nkuti aneneri awo amawadzera ndi zozizwitsa, 
koma iwo adawatsutsa ndi kuwanyoza. 

Kenako surayi yathetsa bodza la osakhulupirira m'kunena 
kwawo kwakuti sadzauka ku imfa. Ndipo yawapempha anthu 
kuti akhulupirire Mulungu pamodzi ndi Mtumiki Wake ndi 
kuunika kumene kudavumbulutsidwa kwa iye. Ndiponso 
yawachenjeza za tsiku lamsonkhano waukulu; tsiku limene 
kudzaonekera poyera kulephera kwa anthu osakhulupirira. 

Koma amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino, 
kupambana kwakukulu kudzakhala pa iwo. Ndipo 
osakhulupirira adzakhala eni moto. Yafotokozanso kuti mavuto 
amachitika kupyolera mchifuniro cha Chauta ndi kuti amene 
akhulupirira Mulungu akuongola mtima wake. 

Yawapemphanso anthu surayi kuti amvere Mulungu ndi 
Mthenga Wake. Ndipo okhulupirira yawauza kuti chuma ndi ana 
awo ndi mayeso. Asasiye chimene alamulidwa kuchichita 
potanganidwa ndi chuma ndi ana. Ndipo yamaliza ndi kuwauza 
kuti apereke chuma chawo panjira yabwino, ndi kuti Iye 
Ngoyamika, Ngodekha, Ngodziwa zam'mseri ndi zoonekera 
poyera. Adzawalipira pazimene akupereka pa njira Yake. 

Iye Ngopambana ndipo sapambanidwa; Ngwanzeru ndipo 
sachita zopanda pake. 



Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 I 1227 TA^i 



n t jjuJi 5jj-a 



Surat At-Taghabun LXIV 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Zonse zakumwamba ndi 
zam'dziko Lapansi zikulemekeza 
Mulungu (ndi Kumyeretsa ku 
zinthu zosayenerana ndi 
Ulemerero Wake; Ufumu Ngwake 
ndipo Kutamandidwa kwabwino 
Nkwake. Ndipo lye ali ndi 
mphamvu pa chilichonse. 

2. lye ndiAmene adakulengani 
(Nonsenu popanda kuchokera ku 
Chilichonse) choncho mwa inu 
alipo Wosakhulupirira (Mulungu 
wake) ndiponso Mwa inu alipo 
wokhulupirira. Ndipo Mulungu 
Ngopenya zonse zimene 
Mukuchita (ndipo adzakulipirani 
nazo). 

3. Adalenga thambo ndi nthaka 
Mwachoonadi ndipo 
adakujambulani Majambulidwe 
abwino; Ndipo Kobwerera nkwa 
lye (pa tsiku Lachiweruziro). 

4. (Mulungu) akudziwa 
zakumwamba ndi Zam'dziko 
lapansi, ndiponso akudziwa 
Zimene mukuzibisa ndi zimene 
Mukuzilengeza (zochita ndi 
Zoyankhula); Mulungu Ngodziwa 
Zam'zifuwa. 



^ "^ : - - : ^ ==== ^Z_ 



oJ&3\^3\&\j 



-^ 












© 



ffri" *£'■ 



*<1t ' »< -c 






9*A 



®^daH 



Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 I 1228 I Y A t> 



^ i ^ttsJt 5jj-- 



5. Kodi siidakufikeni nkhani ya 
omwe Sadakhulupirire kale? 
Adalawa (Zowawa) zazoipa za 
zinthu zawo (Padziko lapansi). 
Ndipo chilango Chowawa 
chidzakhala pa iwo (tsiku Lomaliza). 

6. Zimenezo nchifukwa chakuti 
atumiki Awo amawadzera ndi 
zozizwitsa koma Iwo amanena 
(mwachipongwe) c Ha! Anthu 
anzathu (onga ife) angationgole?' 
Choncho sadakhulupirire (utumiki 
Wawo) ndipo adanyoza (choonadi) 
Potero Mulungu adawasiya (ndi 
Kupanda chikhulupiriro kwawo) 
ndipo Mulungu ngokwanira 
ndiponso Ngoyamikidwa. 

7. Amene sadakhulupirire 
akumanama kuti Sadzaukitsidwa 
ku imfa. Nena (kwa Iwo iwe 
Mtumiki{SAW}): "Sizili choncho 
Pali Mbuye wanga, ndithu 
Mudzaukitsidwa ku imfa, ndipo 
Mudzauzidwa zimene mumachita 
(Padziko lapansi). Zimenezo kwa 
Mulungu nzofewa nzosavuta 
(kuzichita)" 

8. Khulupirirani Mulungu ndi 
Mtumiki Wake, ndi dangalira 
limene Talivumbulutsa. Ndipo 
Mulungu Ngodziwa kwambiri 
zimene mukuchita. 

9. (Kumbukirani) tsiku limene 
Adzakusonkhanitsani chifukwa 















^j^Maftss 



Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 | 1229 | Y A »>i % t ^udi 5^ 



cha Tsiku lakusonkhana 
(zolengedwa Zonse), limenelo ndi 
tsiku lolephera; Ndipo amene 
akhulupirira mwa Mulungu ndi 
kuchita zabwino, Anfafanizira 
zoipa zake, ndipo Akamulowetsa 
m'minda momwe Pansi pake 
pakuyenda mitsinje; Adzakhala 
m'menemo muyaya; Kumeneko 
ndiko kupambana Kwakukulu. l 

10. Koma amene 
sadakhulupirire natsutsa 
Zozizwitsa Zathu (zimene 
Zidaperekedwa kwa Aneneri 
Athu;) Iwowo ndi anthu akumoto; 
adzakhala Mmenemo muyaya 
amenewo Ndiwo mabwerero oipa. 

11. Palibe vuto lililonse 
lingapezeke Pokhapokha Mulungu 
atafuna; ndipo Amene akhulupirira 
Mulungu, (Mulungu) aongola 
mtima wake (kuti Ukhale 
wokhutira ndi chiweruzo cha 
Mulungu). Ndipo Mulungu 
Ngodziwa Chinthu chilichonse. 

12. Choncho mverani Mulungu 
ndipo Mverani Mtumiki ngati 
munyozera, (Ndi zanu), ndithu 
udindo wa Mtumiki Wathu 
ndikufikitsa uthenga Omveka. 






t>i 












Tsiku lolephera: Akafiri adzakhala olephera chifukwa cha kusakhulupirira 
kwawo. Nawonso Asilamu aulesi adzakhala olephera chifukwa cha 
kusakwaniritsa kwawo malamulo a Mulungu. 



Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 I 1230 I * A *>» 



1 i jjUsIi *jj-' 



13. Mulungu, palibe wina 
wopembedzedwa Mwachoonadi 
koma lye. Ndipo kwa Mulungu 
Yekha, okhulupirira atsamire. 

14. E, inu amene 
mwakhulupirira! Ndithu Ena mwa 
akazi anu ndi ana anu Ndi adani 
anu (chifukwa chakuti 
Amakuchotsani kumbali yomvera 
Mulungu pofuna kuti 
mukwaniritse Zofuna zawo). 
Chenjerani nawo. Ngati 
Muwakhululukira ndi 
kunyalanyaza Ndi kubisa zolakwa 
zawo ndibwino Kwambiri, ndithu 
Mulungu Ngokhululuka, 
Ngwachisoni. 1 

15. Ndithu, chuma chanu ndi 
ana anu Ndimayeso (kwa inu); 
koma kwa Mulungu kuli malipiro 
aakulu (Kwa yemwe wasankha 
kumvera Mulungu). 

16. Choncho muopeni Mulungu 
Mmene mungathere mverani 
(Zophunzitsa Zake) ndipo tsatirani 
(Malamulo Ake) komanso 
perekani Zimene wakupatsani 



$&fr&&$pm 















1 (Ndime 14-15) Pakufunika kuti munthu akhale ndi muyeso wabwino. Chinthu 
chilichonse achipatse choyenera chake. Nthawi zambiri kumapezeka kuti 
munthu amalakwira Chauta chifukwa cha kufunitsitsa chuma, kapena 
chifukwa chofuna kukondweretsa ana ake ndi mkazi wake ndi kunyalanyaza 
malamulo a Mulungu. Choncho apa, chuma Chake, ana ake ndi mkazi wake 
amasanduka adani ake okamuika m'mavuto kwa Mulungu. Nkofunika kwa 
munthu kukondweretsa Mulungu ndi kumkonda asanakondweretse ndi 
kukonda china chilichonse. 



Surat 64. At-Taghabun Juzu 28 



1231 



YA^>l 



*\ i ji\xS\ djj-*» 



zikhala zabwino Kwa inu. 
Dzichitireni nokha zabwino. Ndipo 
amene watchinjirizidwa ku 
Umbombo wake, iwowo ndiwo 
Opambana. 

17. Ngati mungamkongoze 
Mulungu Ngongole yabwino 
aiwonjezera kwa inu (Malipiro 
ake) ndipo akukhululukirani 
(Zolakwa zanu.) Ndipo Mulungu 
Ngolandira kuthokoza, Ngoleza. 

18* Ngodziwa zobisika ndi 
zoonekera; Ngwamphamvu 
zopambana; Ngwanzeru Zakuya. 



jWy8ca#&iui£<$i 



%s&fcm& 



y**j 



© 



jp&fi^fi^j^^ 




Surat 65. At-Talaq Juzu 28 



1232 



TA^>l 



Id j^UaJl Ojj^ 




Surayi ikufotokoza ena mwamalamulo osiyanirana ukwati 
kudzanso edda ndi mitundu yake ndi malamulo ake polongosola 
kuti mkazi wa edda akhale panyumba pomwepo pomwe 
wasudzulidwapo. Ndi kuti apatsidwe zofunika pa moyo wake, 
monga chakudya ndi pogona. 

Pakuti polongosola malamulo amenewa, monga momwe ilili 
njira ya Qur'an pali lonjezo labwino kwa amene akutsatira 
malamulo a Mulungu; ndi lonjezo la chilango kwa amene 
akupyola malirewo. Kenako yaloza zotsatira za odzitukumula 
posiya kutsatira malamulo a Chauta ndi Aneneri Ake. Ndipo 
yatsiriza ndikuwalimbikitsa Asilamu zoopa Mulungu ndi 
kukumbukira chisomo cha Chauta powatumizira Mneneri wake 
amene akuwawerengera ndime za Mulungu kuti awatulutse 
mumdima ndi kuwaika m'kuunika. Ndiponso yafotokoza 
mphamvu Zake zazikulu polenga thambo zisanu ndi ziwiri ndi 
nthakanso chimodzimodzi. 




Surat 65. At-Talaq Juzu 28 



1233 



YA*>I 



\0 JtAiail djj- 



Surat At-Talaq LXV 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. E, iwe Mneneri(SAW) ngati 
Mufuna kusudzula akazi ukwati, 
Asudzuleni mnyengo yowerengera 
Edda yawo (kuwerengera edda 
Kumayambika mkazi akakhala ndi 
Twahara akachira matenda 
akumwezi), Ndipo werengerani 
nyengo ya edda. Ndipo Muopeni 
Mulungu Mbuye wanu. Ndipo 
Musawatulutse m'nyumba zawo 
Ndiponso asatuluke kupatula 
Akachita tchimo lalikulu loonekera 
(Loyenera chilango, apo atha 
Kutulutsidwa). Ndipo amenewa 
ndiwo Malire a Mulungu (amene 
Wawakhazikitsa kwa anthu Ake). 
Ndipo Amene apyola malire a 
Mulungu Wadzichitira yekha zoipa. 
Sukudziwa (Cholinga cha malamulo 
amenewa) Mwina Mulungu 
adzadzetsa chinthu Pambuyo pake 
(chosonyeza kuyanjana). 

2. Ngati osiyidwawo nyengo 
yawo (edda) Itayandikira kutha, 
abwerereni mwa Ubwino kapena 
asiyeni mwaubwino (Polekerera 
nyengoyo kuti ithe); ndipo 
(Powabwerera) funani mboni 
ziwiri Zolungama zochokera mwa 
inu (zimene Zichitire umboni kuti 









^^^^saai 



o&&\<jp$\&\j>. 









Surat 65. At-Talaq Juzu 28 



1234 



tA^jJrl 



n o JtAkJl 5j^ 



inu mukubwererana) Ndipo 
perekani umboni chifukwa choopa 
Mulungu. Zimenezo ndizo 
akulangizidwa Nazo amene 
akhulupirira mwa Mulungu Ndi 
tsiku lomaliza.Ndipo amene 
akumuopa Mulungu (potsatira 
malamulo Ake), Amkonzera njira 
yotulukira (m'mavuto). 

3. Ndipo ampatsa riziki 
kuchokera momwe 
Samayembekezeramo. Ndipo 
amene Akutsamira kwa Mulungu 
(pa zinthu zake Zonse), ndiye kuti 
Mulungu ali wokwana Kwa iye 
(kumkonzera chilichonse), ndithu, 
Mulungu Ngokwaniritsa cholinga 
Chake ndi Chofuna Chake. Ndithu, 
chinthu chilichonse Mulungu 
wachipatsa mlingo wake 
Woyenera (ndipo sichingaupyole). 

4. Ndipo edda ya amene asiya 
kudwala Kumwezi mwa akazi anu 
chifukwa cha Kukula, ngati 
mukukaika (nthawi Ya edda 
yawo), edda yawo ndi miyezi Itatu. 
Ndi omwe sadathe msinkhu edda 
Yawo ndi momwemonso. Tsono 
akazi Apakati nthawi yothera edda 
yawo Ndipomwe abereka. Ndipo 
amene aopa Mulungu amfewetsera 
zinthu zake. (Kuti zikhale zosavuta.) 

5. Limenelo ndilamulo la 
Mulungu (Lomwe) walikhazikitsa 
kwa inu. Ndipo amene aopa 












Surat 65. At-Talaq Juzu 28 



1235 



TAf>l 



10 (j^UaJl djj~> 



Mulungu (Posunga malamulo ake), 
Amam'fafanizira zoipa zake, 
ndiponso Amamkulitsira malipiro 
ake. 

6. Akhazikeni (osiyidwawo) 
m'mene Mukukhala inumo monga 
momwe kulili Kupeza kwanu (ndi 
mphamvu Zanu ngakhale kuti 
mwawasiya ukwati). Musawavute 
ndi cholinga chowapana (Kuti 
athawe okha). Ngati ali ndi pakati, 
Apatseni zonse zofunika pa moyo 
Mpaka adzabereke. Ngati 
akukuyamwitsirani ana anu 
apatseni malipiro awo Mokwanira; 
gwirizanani pakati panu 
Mwaubwino ndi mofatsa. Ngati 
wina Apereka mavuto kwa mnzake 
(ndiye Kuti mwanayo) 
adzamuyamwitsira (Mkazi) wina, 

7. Wopeza bwino apereke 
malinga ndi Kupeza bwino kwake; 
ndipo amene Wachepekedwa riziki 
lake, apereke (Kangachepe) 
pazomwe Mulungu 
Wampatsa. Mulungu sakakamiza 
aliyense Kupatula zomwe ampatsa. 
Mulungu apereka Kupeza bwino 
pambuyo pa masautso. 

8. Eni midzi yambiri adanyoza 
lamulo La Mbuye wawo ndi 
Aneneri Ake, Ndipo 
tidawawerenga ndi chiwerengero 
Chokhwima (posanthula zochita 
zawo Zonse). Ndiponso 
tidawalanga ndi Chilango chaukali. 












o 1 



Surat 65. At-Talaq Juzu 28 I 1236 I * A *>i 



10 J^UaJl 5jj-» 



9. Choncho adalawa kuipa kwa 
zinthu Zawo ndipo mapeto azinthu 
zawo adali Kutayika (kuonongeka 
kwakukulu), 

10. Mulungu wawakonzera iwo 
chilango Chopweteka choncho, 
muopeni Mulungu, Ee, inu eni 
nzeru, amene mwakhulupirira, 
Ndithu, Mulungu wavumbulutsa 
Chikumbutso (Cholemekezeka 
kwa inu). 

11. Mtumiki (amene) 
akukuwerengerani Ndime za 
Mulungu zolongosola (Choonadi ndi 
chonama) kuti Awatulutse 
mumdima ndi kuwaika Ku dangalira 
amene wakhulupirira ndi Kumachita 
zabwino. Ndipo amene Akhulupirira 
Mulungu ndi kumachita Zabwino, 
adzamlowetsa m'minda Momwe 
mitsinje ikuyenda pansi pake; 
Akakhala m'menemo muyaya. 
Ndithu Mulungu wamkonzera 
riziki (dalitso) Labwino (Jannah) 1 

12. Mulungu ndiYemwe 
adalenga thambo Zisanu ndi ziwiri, 
nthakanso Chimodzimodzi. 
Malamulo Ake akutsika Pakati pa 
izo kuti mudziwe kuti ndithu, 
Mulungu pachilichonse ndi 
Wokhoza Ndikutinso Mulungu 
wachizinga Chilichonse 
m'kuchidziwa. 












%$&$* 









t \'A %>'*•*& 



1 Riziki ndi mawu a Chiarabu amene akutanthauza chilichonse chimene 
chimathandiza 



Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1237 



tA *>■» 



*\ *\ f.j*d\ «JJ~*» 




Surayi ikuloza zina zimene zidamkwiyitsa Mtumiki (SAW) 
mwa akazi ake. Choncho adadziletsa kuchita zina 
mwazosangalatsa zomwe Chauta adamloleza. Ndipo wachenjeza 
akazi ake pazimene iwo adachita. 

Kenaka surayi ikulamula okhulupirira kuti adzitchinjirize 
okha ndi mawanja awo kumoto umene nkhuni zake ndi anthu 
ndi miyala. Ndipo yafotokoza kuti Mulungu sadzavomereza 
madandaulo a anthu osakhulupirira pa tsiku lomaliza. 

Kenaka ikuwayitana okhulupirira kuti alape kwa Mulungu 
mwachoonadi. Ndipo ikuitananso Mneneri kuti achite Jihad 
yaikulu pa anthu osakhulupirira ndi achinyengo ndi kutinso 
awaumire mtima. 

Surayi yatsiriza ndikupereka mafanizo ofotokoza kuti ubwino 
wa mwamuna pabanja sungapulumutse mkazi ngati ali wopotoka 
pa chipembedzo cha Mulungu. Ndipo ubwino wa mkazi pabanja 
sungapulumutse mwamuna wake ku chionongeko ngati 
mwamunayo ali wosokera pa chipembedzo cha Chauta. 




Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1238 



YAtjA-i 



1% f.f*A\ «jj-» 



Surat At-Tahrim LXVI 



f g^::'^m : 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. E, iwe Mneneri(SAW) 
nchifukwa ninji Ukudziletsa 
chimene Mulungu Wakuloleza 
kuchita? Ukufuna kukondweretsa 
akazi ako (nchifukwa Chake 
wachita izi?) Koma Mulungu 
Ngokhululuka kwambiri 
Ngwachisoni. 

2. Ndithu, Mulungu 
wakhazikitsa Kamasulidwe 
kakulumbira Kwanu, ndipo 
Mulungu Ndiye Mtetezi wanu, lye 
Ngodziwa Kwambiri ndiponso 
Ngwanzeru zakuya (Pamalamulo 
amene wawakhazikitsa Kwa Inu). 1 

3. Ndipo kumbuka pamene 
Mneneri(SAW) Adauza wina mwa 
akazi ake nkhani 

Mwachinsinsi,choncho (mkaziyo) 
Pamene adaiulula, Mulungu 



o&£\&$\&\j 



-^ 






J? 9 &9l< 









1 Mkazi ndimkazi basi. Mtumiki adanena m'Mahadisi kuti sipadapezeke mkazi 
amene ali wokwanira pa chinthu chilichonse kuyambira pamene dziko 
tidayamba mpaka kutha kwake kupatula akazi anayi basi. Iwowa ndi awa: 
Mayi Fatuma, Mayi Khadija, Mayi Mariam (Maria) ndi mayi Asiya (mkazi wa 
Farawo). Kusakwanira kwa akazi pa chilichonse kumapezekanso ngakhale 
mwa akazi a Mtumiki, amamsautsa Mtumiki pomuchitira nsanje ngakhale kuti 
iwo amapemphera kwambiri, kawirikawiri makamaka amayi awiri awa Mayi 
Aisha ndi Mayi Hafsa monga momwe zilili m'ndime 4 ya sura iyi. Mulungu 
wawakalipira kwambiri m'ndime 5 ya sura yomweyi ndi m'ndime 28 ya surat 
Ahzab. Koma adalapa mwachangu ndipo Mulungu adawayanja monga zilili 
m'ndime 52 ya Surat Ahzab. 



Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1239 I ™>>> 



n *\ f.y*A\ *jj-* 



Adamdziwitsa (Mtumiki) za 
kuululidwa Kwa nkhaniyo, (ndipo 
Mtumiki) Adaifotokoza mbali ina 
ya nkhaniyo, Koma mbali ina 
adaisiya. Pamene Adamfotokozera 
(mkazi wake) Zankhaniyo adati: 
"Ndani wakuuza Zimenezi?" 
(Mtumiki{SAW}) adati: 
"Wandiuza Wodziwa 
kwambiri.Ndiponso Wodziwa 
zazing'ono ndi zazikulu (Amene 
sichibisika kwa lye Chobisika 
chilichonse.) 

4. (Amene adali ndi nsanje 
kwambiri mwa Akazi ake ndi mayi 
Aisha ndi mayi Hafsa. Ndipo 
Mulungu adawauza Motere): 
"Ngati awirinu mulapa kwa 
Mulungu pazimene mwachita 
(chitani Changu kulapa) chifukwa 
chakuti Mitima yanu yapotoka 
pang'ono (Chifukwa cha nsanje pa 
zimene Mneneri akufuna zosunga 
chinsinsi Chake); koma ngati 
awirinu Muthandizana pazimene 
zingamvutitse Ndithu, Mulungu 
ndiye Mtetezi wake Ndi Jibulilu 
(Gabriel). Ndiponso Asilamu 
abwino; naonso angelo, 
Kuonjezera apa ndiathandizi (ake). 

5. Ngati (Mtumiki) 
akakusuzulani, ndithu Mbuye 
wake, ampatsa akazi ena m,malo 
Mwa inu, abwino kuposa inu: 
Ogonjera (Mulungu), okhulupirira 









OjO 



, --,-- '*v~H ''tsfr- KT- 

-*' • -" <?*• 2 * V * V <4> " ft- 



Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1240 



TA t>i 



*\*\ fLJ*A\ Sjj-** 



(ndi mitima Yawo), omvera, olapa, 
odzichepetsa (Pamaso pa Mulungu 
ochita mapemphero Kwambiri), 
oyenda (pa chikhulupiriro Cha 
Mulungu kapena ochulukitsa 
Kumanga) amene adakwatiwapo 
Kale ndi osakwatiwapo." 

6. E, inu amene 
mwakhulupirira! Dzitchinjirizeni 
inu ndi mawanja anu Ku moto 
umene nkhuni zake ndi anthu Ndi 
miyala; oyang'anira ake ndi 
Angelo ouma mtima, amphamvu: 
Sanyoza Mulungu pa zimene 
Wawalamula, amachita (zokhazo) 
Zimene alamulidwa. 1 

7. (Adzawauza osakhulupirira 
pa tsiku Lachiweruzo) E, inu 
amene Simdakhulupirire! 
Musadandaule lero, Ndithu 
mukulipidwa pa zimene 
Mumachita (padziko lapansi). 

8. E, inu amene 
mwakhulupirira! Lapani kwa 
Mulungu; kulapa koona; Ndithu 
Mbuye wanu akufafanizirani Zoipa 
zanu ndi kukakulowetsani 
M'minda momwe mitsinje 
ikuyenda Pansi pake, tsiku limene 
Mulungu Sadzayalutsa mtumiki 
ndi amene Adakhulupirira 












Akuluakulu ndiponso aliyense amene ali ndi udindo akuwalamula 
kuwakonza amene ali pansi pawo powaphunzitsa chipembedzo ndi 
chikhalidwe chimene Mulungu akuchifuna kuti awatchinjirize ku chionongeko. 
Ngati satero ndiye kuti chilango chikafika chidzakhala cha onse. 



Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1241 



XA frjJt-* 



%n {.y*A\ 5jj-*» 



pamodzi naye. Dangalira lawo 
lidzayenda chapatsogolo pawo ndi 
mbali yakumanja Kwawo, uku 
akunena: "Mbuye wathu! 
Tikwanitsireni dangalira lathu 
(Mpaka likatifikitse ku munda wa 
Mtendere), ndiponso 
tikhululukireni Ndithu Inu ndi 
Okhoza chilichonse." 

9. E, iwe Mneneri! Limbana ndi 
Akafiri (Osakhulupirira) ndi 
Amunafikina (Achinyengo), 
aumire mtima.Ndipo malo Awo 
ndi ku Jahannama,taonani kuipa 
Kobwerera (kwawo)! 

10. Mulungu wapereka fanizo la 
Osakhulupirira monga mkazi wa 
Nuhu Ndi mkazi wa Luti.Awiriwa 
adali pansi Pa akapolo Athu awiri 
abwino, koma Adali 
osakhulupirika kwa amuna awo, 
(Ndipo amuna awo) sadawateteze 
Kalikonse ku chilango cha 
Mulungu, Ndipo kudanenedwa 
kwa iwo "Lowani Ku moto 
pamodzi (ndi ena) olowa". 

11. Ndiponso Mulungu 
wapereka fanizo la Amene 
akhulupirira monga mkazi wa 
Firiauna (Farawo) pamene 
adanena: "Mbuye wanga! 
Ndimangireni, kwa inu, Nyumba 
mu Jannah, ndipo ndipulumutseni 
Kwa Firiauna ndi zochita zake, 



<§8^##efiBaK 









!Cy&J 






v^&<&&&& 



Surat 66. At-Tahrim Juzu 28 



1242 



YA tjJrl 



i n ^ytsJi «jj-- 



ndiponso Ndipulumutseni kwa 
anthu oipa (Ndi amtopola.)" 

12* Ndi (fanizo lina la 
wokhulupirira monga) Mariam 
mwana wa Imran amene adasunga 
Umaliseche wake; ndipo tidauzira 
mmenemo Mzimu Wathu ndipo 
adavomereza mawu a Mbuye wake 
(omwe adali zolamula Zake ndi 
Zoletsa Zake) ndi mabuku Ake 
(amene Adavumbulutsidwa kwa 
Aneneri Ake); adali Mmodzi wa 
opitiriza kudzichepetsa (ndi 
Kumvera Mulungu). 



'f 1^6't* "^l*'! 







Surat 67. AI-Mulk Juzu 29 I 1243 I Y ^ *>» 



nv dWiajj-* 




Surayi ikutchedwa Surat Mulk ndipo tanthauzo lake ndi 
Ufumu. Yalandira dzina limeneli chifukwa chakuti mu aya 
(mundime) yoyambirira mwatchulidwa mawu a ufumuwa. 

Zolinga zake zenizeni ndikutembenuza maganizo ndipo maso 
kuti apenye zisonyezo zamphamvu ya Mulungu yoposa, 
m'mitima ndi padziko lonse, kumwamba ndi pansi; kuti 
kuyang'ana kumeneko kukhale njira yokhulupirira mwa 
Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndiponso ikulongosola zimene 
zikawachitikira okana pamene azikaponyedwa ku Jahena 
ndikumva mkokomo wake m'menemo uku ali kupsa. Tsiku 
limenelo adzavomereza zolakwa zawo pamodzi ndi kudandaula 
kwawo posalabadira za moyo wa tsiku lomaliza. 

Izi zikachitika pamene angelo azikawafunsa mafunso 
owadzudzula onena kuti: "Kodi sadakudzereni Aneneri ndi 
kukuitanirani kwa Mulungu ndi kukuchenjezani za tsikuli?" 

Koma amene adaopa Mbuye wawo ndi kumkhulupirira 
akalandira chikhululuko pazimene adalakwa ndi malipiro aakulu 
pazimene adachita zabwino. 




Surat 67. Al-Mulk Juzu 29 



1244 



y<\ t&\ 



W diilloj^ 



Surat Al-Mulk LXVII 



* 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Watukuka ndi kudalitsika 
Amene M'manja Mwake muli 
Ufiimu (Wochita Chilichonse 
pazolengedwa zonse); ndipo lye ali 
ndi mphamvu yokwanira 
Pachilichonse. 

2. Amene walenga imfa ndi 
moyo kuti Akuyeseni (mayeso) 
ndani mwa inu Ali wochita 
zabwino (kwambiri). Ndipo lye 
ndiWopambana m'mphamvu, 
(Salephera kanthu); ndiponso 
Wokhululukira (olakwa). 2 

3. Amene adalenga thambo 
zisanu ndi Ziwiri mosanjikana 
(kapena zolingana Mkalengedwe 
kake). Suona kusiyana M'zolenga 
za Wachifundo chambiri. Bwereza 
kuyang'ana; kodi ukuona Pena 
pong'ambika? 



o&£\<&&\&\** 



J^ 












Sura imeneyi, Mtumiki (SAW) amafuna kuti Msilamu atiyense ailoweze 
pamtima ndi kuzindikira bwino tanthauzo lake. Mtumiki (SAW) adali ndi 
chizolowezi chomawerenga surayi asanagone. M'sura imeneyi muli 
chikumbutso chosonyeza kuti Mulungu Ngwamphamvu amachita mmene 
angafunire. Chimene wafuna chichitika ngakhale anthu sakufuna. Ndipo 
chimene sanafune kuti chichitike sichingachitike ngakhale anthu atafunitsitsa 
kuti chichitike. Zonse zakumwamba ndi zam'nthaka ndi Zake. 
2 M'ma aya awa:- Ambuye Mulungu akutilangiza kuti tikhale oganizira zomwe 
adalenga zimene zingatisonyeze nzeru Zake ndi mphamvu Zake zakuya. 
Tilingalire m'zolengedwa Zake, tisalingalire mwa lye mwini chifukwa sitingathe 
kumlingalira mmene alili pomwe tikulephera kuulingalira mzimu wathu momwe 
ulili. 



Surat 67. Al-Mulk Juzu 29 | 1245 "] T 1 *>i 



nv liiiit Sjj^ 



4. Bwerezanso kuyang'ana 
kachiwiri, Kuyang'anako 
kukubwerera wekha (Uku maso) 
ali olobodoka ndiponso Otopa. 
(Suona polakwika paliponse). 

5. Ndipo ndithu, talikongoletsa 
thambo Loyandikirali ndi nyali 
(nyenyezi) ndipo Tazichita 
kukhala (mochokera zenje) 
Zolasila asatana. Ndipo 
tawakonzera (Patsiku lomaliza) 
chilango Chamoto woyaka. 

6. Ndipo kwa amene 
sakhulupirira Mbuye Wawo ali 
nacho chilango cha Jahannama; 
Ndipo kuipirenji kobwerera! 

7. Akadzaponyedwa 
M'menemo adzamva Mavume ake 
(oipa) uku ukuwira Mwaukali. 

8. Udzayandikira kuphwasuka 
chifukwa Cha mkwiyo (kukwiira 
oipa); nthawi Iliyonse gulu (la 
oipa) likadzaponyedwa 
M'menemo, Angelo oyang'anira 
Motowo adzawafunsa 
(mowadzudzula); "Kodi 
sadakufikeni mchenjezi 
(Wokuchenjezani za tsikuli?)." 

9. Adzayankha "Inde, adatifika 
mchenjezi Koma tidatsutsa, ndipo 
tidati Mulungu Sadavumbulutse 
chilichonse (kwa iwe Ngakhale 
kwa anzako). Koma inu muli 
M'kusokera kwakukulu". 












(£$ to^S ^i £^^gly5 1 13^ 












®M$° 



Siirat 67. AI-Mulk Juzu 29 



1246 I "*>i 



nv ^uiiSj^ 



10. Ndipo adzanena: 
"Tikadakhala kuti Tidamvera 
(zimene ankatiuza) kapena 
Kuziganizira mwanzeru 
sitikadakhala M'gulu la anthu 
akumoto. 

11. Choncho adzavomereza 
machimo awo (Koma sipadzakhala 
chopindula;) Kuonongeka ndi 
kukhala kutali (ndi Chifundo cha 
Mulungu) kuli pa anthu Akumoto! 

12. Ndithudi amene akumuopa 
Mbuye Wawo pomwe iwo 
sakumuona, Adzapeza 
chikhululuko pa machimo Awo ndi 
malipiro aakulu (pa zabwino 
Zomwe ankachita). 

13. Ndipo bisani mawu anu, 
kapena aonetseni Poyera; (zonsezi 
nchimodzimodzi kwa Mulungu) 
ndithudi lye Ngodziwa Zobisika 
zam'mitima. 

14. Kodi asadziwe amene 
adalenga (zinthu Zonse)? Pomwe 
lye Ngodziwa zinthu 
Zingo'nozing'no kwambiri mmene 
zilili (Ndiponso) Ngodziwa nkhani 
zonse. 

15. lye ndi Amene 
wakupangirani nthaka kuti Ikhale 
yogonjera (pachilichonse chimene 
Mufuna). Choncho yendani mbali 
zake Zonse; ndipo idyani riziki 
lam'menemo, (Limene Mulungu 









%^^^&&- <aW Si 









i&g\$$\&cFv>$j$ 









Surat 67. Al-Mulk Juzu 29 I 1247 I * * *>* 



%V dUll 5j>- 



akukutulutsirani). Ndipo Kwa lye 
yekha ndiko kobwerera kwanu 
(Nonse mtapatsidwa moyo 
wachiwiri). 

16. Kodi muli m'chitetezo kwa 
Amene ufumu Wake uli 
kumwamba kuti Sangakukwirireni 
m'nthaka (Ndikukudzidzimutsani) 
pamene Nthaka ikugwedezeka 
molimba? 

17. Kapena muli m'chitetezo 
kwa Amene Ufumu Wake uli 
kumwamba kuti Sangakutsitsireni 
mphepo yamkuntho ya Miyala (ndi 
kukuonongani ndi miyalayo?) 
Choncho mdzadziwa mmene lilili 
chenjezo Langa (pa inu). 

18. Ndithudi amene adalipo 
kale iwo Asanabadwe adakana 
mithenga yawo. Nanga udali 
bwanji mkwiyo Wanga pa Iwo 
(pakuwaononga onse)! 

19. Kodi,sadaone mbalame 
pamwamba pawo Mmene 
zikutambasulira (mapiko awo) ndi 
Kuwafiimbata. Palibe amene 
akuzigwira Kuti zisagwe koma 
(Mulungu) Wachifundo chambiri; 
ndithudi lye Pachilichonse 
Ngopenya 

20. Kodi ndani amene ali 
asilikali anu Okutetezani 
kuchilango posakhala (Mulungu) 
Wachifundo chambiri? Ndithudi 



^O ^)\ f&&\ (X&^V* 



&j&a\v$jffl'j^ 






^J^(^2^ivwU4iIj 



©. 









Siirat 67. Al-Mulk Juzu 29 



1248 



y* *>i 



IV viJLili $jj-» 



osakhulupirira Ali mchinyengo 
(pazimene akuganizira). 

21. Kodi ndani angakupatseni 
riziki (Limene mungakhalire ndi 
moyo ndi Kupezera mtendere) ngati 
lye Atatsekereza riziki lake (kwa 
inu)? Koma Akafiri akupitiriza 
kudzikweza Kwawo,ndi kudziika 
kutali ndi choonadi. 

22. Kodi amene akuyenda 
mozyolika ndi Nkhope yake 
angakhale woongoka Kapena 
amene akuyenda molungama 
Panjira yosakhota? 

23. Nena: "lye ndi Amene 
adakulengani (Pomwe simudali 
kanthu) ndipo Adakupatsani 
makutu, maso ndi mitima, (Zimene 
mukhoza kupeza nazo mtendere): 
Koma kuyamika kwanu (kwa 
Yemwe Adakupatsani zimenezi) 
Nkochepa kwambiri. 

24. Nena: "lye ndi amene 
adakuchulukitsani Padziko ndipo 
kwa lye (yekha) ndiko 
Mudzasonkhanitsidwa (kuti 
Adzakuwerengereni ndi 
kukulipirani). 

25. Akunena (osakhulupirira za 
kuuka Monyada): "Ndiliti 
(lidzakwaniritsidwa) Lonjezo ili 
ngati inu muli oona?" 

26. Nena (iwe MtumikijSAW}): 
"Ndithu Kudziwa (kwa izi) nkwa 















©, 



* **&.■. 



'OX 



^jmx>^$ 









Qca^usftWica* 



Surat 67. Al-Mulk Juzu 29 



1249 



n *>» 



"VV dlill s^ 



Mulungu yekha: Ndipo ndithudi ine, 
ndine mchenjezi Wowonekera." 

27. Koma akadzaziona (zimene 
Akulonjezedwazo) zili pafupi (ndi 
Iwo), nkhope za amene 
sadakhulupirire Zidzakhumudwa 
ndikuyaluka kwambiri Ndipo 
kudzanenedwa (mowadzudzula); 
"Izi ndi zija mudali kuzipempha 
(Kuti zidze, zadza tsopano). 

28. Nena (iwe 
Mtumiki{SAW}): "Tandiuzani 
Ngati Mulungu atandiononga 
pamodzi Ndi amene ndili nawo 
(monga momwe Mukufunira) 
kapena kutichitira chifundo 
(Ndikutalikitsa nthawi ya moyo 
wathu). Nanga ndani amene 
adzawateteza Wosakhulupirira ku 
chilango Chowawa?" 

29. Nena: "lye ndiye (Mulungu) 
Wachifiindo chambiri, 
takhulupirira mwa lye ndiponso 
kwa lye ndikumene tatsamira. 
Posachedwapa mudziwa (chilango 
Chikatsika kuti) ndani (m'magulu 
Awiriwa) yemwe ali m'kusokera 
Koonekera." 

30. Nena: "Tandiuzani ngati 
madzi Anuwa ataphwa 
(kulowerera pansi Penipeni); 
choncho ndani amene 
Angakubweretsereni madzi oyenda 
(Ochokera mkati mwanthaka?). 



$ 9 &<?*-< 






&V*i 4»I(^U| t)lfttol J» 









Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 



1250 



Y<* >>i 



*VA ^JLaJl 5jj~- 




M'sura yolemekezekayi muli mawu othondoza Mneneri 
(SAW) ndi kulirimbikitsa khama lake kuti apitirire kuchita 
choonadi popanda kugonjera aliyense. 

Mulinso fanizo la chilango chomwe chidawagwera eni 
mzinda wa Makka monga chilango chomwe chidawagwera eni 
munda amene nkhani yawo yakambidwa M'surayi. Ndiponso 
ikupereka uthenga wabwino kwa okhulupirira pa zimene 
akalandira kwa Mbuye wawo Mulungu ndikunenetsa kuti palibe 
kufanana pakati pawo ndi osakhulupirira. 

Surayi ikuwakanira otsutsa pazimene ankadzinyenga okha 
popanda choonadi. Ndipo ikuwaopseza polongosola mmene ati 
akakhalire pa tsiku lomaliza. Kenako ikulangiza Mtumiki 
(SAW) kuti apirire. Ndipo yamaliza ndikulemekeza Qur'an 
yolemekezeka. 




Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 1251 t * *j*-i 



nA q&\ 5jj-» 



Surat Al-Qalam LXVIII 



m\i 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nun, Ndikulumbirira pensulo 
(imene Akulembera angelo ndi 
ena), ndi Zimene amalemba. 

2. Pa chisomo cha Mbuye wako 
iwe Sindiwe wamisala (Pokupatsa 
uneneri). 

3. Ndipo ndithu, udzakhala ndi 
malipiro Aakulu osaduka, 
(onkerankera mtsogolo Chifukwa 
cha mavuto amene Ukukumana 
nawo pofikitsa uthenga). 

4. Ndipo ndithu, uli nawo 
makhalidwe abwino Kwambiri 
(omwe Mulungu adakulenga 
Nawo). 

5. Basi, posachedwapa uona, 
Iwonso aona 

6. Kuti ndani mwa inu 
wamisala (iwe kapena Iwo)? 

7. Ndithu, Mbuye wako 
akum'dziwa bwino Amene 
wasokera panjira yake. Ndiponso 
Akuwadziwa bwino Amene ali 
oongoka. 

8. Choncho, usawamvere 
otsutsana; (Usasiye zimene uli nazo 
ngakhale Sakugwirizana nazo). 



o&£\<£&\&\j 



-\j^ 












®&&lpMb 



b 






©Ur&ljX^, 






^Xa&!i.lM 



'- v^ /> ^ 



Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 1252 * * *j*-» 



1A ^JLaSi ojj-- 



9. Akufuna kuti ukadakhala 
Wofewa kwa iwo (pazinthu zina) 
Nawo akadakhala ofewa (kwa iwe) 

10. Ndipo usamumvere aliyense 
wochulukitsa Kulumbira ndiponso 
woyaluka, 

11. Wojeda, woyenda Ndi 
ukazitape, (ndi cholinga 
Choononga umodzi wawo). 

12. Wotsekereza zabwino 
wamtopola Ndipo wamachimo 
ambiri, 

13. Wouma mtima; pamwamba 
pa izi Ndi wodzipachika mu 
mtundu Wa ena, (pomwe iye sali 
m'menemo). 

14. Chifukwa choti iye ndi 
mwini chuma Ndi ana (ndi zimene 
ali kunyadira). 

15. Zikawerengedwa kwa iye 
aya Zathu Amanena: "Izi ndi 
nthano za akale (Ndi zabodza 
zawo, zopeka). 

16. Timuika pamphuno pake 
chizindikiro (Chosasiyana nacho 
kuti ayaluke Nacho pamaso pa 
anthu). 

17. Ndithu ife tidawayesa (eni 
mzinda wa Makka ndi mtendere 
omwe udali pa iwo, Koma adakana 
monga) momwe Tidawayesera eni 
munda, pamene Adalumbira kuti 






%&4&$}&& 



G^'itejSsi 



%;\^m^ 



^ayj£$i 






% 



9[99l\i *[' ij <" 






Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 I 1253 I Y \ *>i 



^A ^JUJt 5jj-- 



akathyola (zipatso za M'munda 
wawozo) mbandakucha (kuti 
Osauka asawaone 
angawapemphe). 

18. Ndipo sadapatule (ngakhale 
wosauka ndi M'modzi yemwe 
ponena kuti uje Timpatse, uje 
tisampatse, kapena Sadanene kuti, 
"Ngati Mulungu afuna)." 

19. Mliri woopsa wochokera 
kwa Mbuye Wako udauzinga 
(mundawo nthawi Yausiku) iwo ali 
mtulo. 

20. Choncho udakhala ngati 
wokoledwa (Chifukwa cha mliri uja). 

21. Adaitanizana nthawi Ya 
mbandakucha. 

22. "Lawirirani kumunda wanu 
kuja ngati Mukufuna kukolola 
(kuopera kuti Angakuoneni osauka)" 

23. Adanyamuka uku 
Akunong' onezana, 

24. (Akunena kuti); 
"Asakulowerereni Osauka lero 
mmenemo". 

25. Ndipo adalawirira ali ndi 
chitsimikizo Choti atha kuwamana 
(osauka). 

26. Choncho pamene adauona, 
adanena (uku Akunjenjemera): 
"Ndithu ife tasokera (Sikuno ayi, 
munda wathu uja suno). 






^^#&fi 



™?t%% 






®^ 9 Ma%^&v\ 






%&^Z$$*&3 






&u^®®&rM 



Siirat 68. Al-Qalam Juzu 29 1254 Y * *>i 



1A ^JUll Sjj~- 



27. Iyayi, ndiwomwewo; koma 
Tamanidwa zinthu zake." 

28. Wolungama mwa iwo 
adanena: "Kodi sindinakuuzeni 
(pamene Mudali kulangizana 
zomana osowa) Kuti bwanji 
osamkumbukira Mulungu (Ndi 
kusintha cholinga chanu)?" 

29. (Iwo) adanena: 
"Alemekezeke Mbuye Wathu 
ndithu ife tidali a chinyengo 
(Chifukwa cha kuipa kwa cholinga 
Chathu)" 

30. Ndipo adatembenukirana 
ndikuyamba Kudzudzulana. 

31. Adati: "E, chionongeko 
chathu ndithu Ife tidapyola malire 
(m' chinyengo chathu) 

32. Mwina Mbuye wathu 
angatipatse Zabwino m'malo mwa 
munda wathuwu. Ndithu ife 
tikufunitsitsa kwa Mbuye Wathu 
(chikhululuko Chake). 

33. Umo ndi mmene 
chimakhalira chilango (Changa 
chomwe ndimachitsitsa Padziko 
lapansi kwa amene Chamuyenera); 
koma chilango cha tsiku Lomaliza 
nchachikulu zedi, akadakhala 
Akudziwa. 

34. Ndithu, oopa Mulungu 
adzakhala ndi Minda ya mtendere 
Kwa Mbuye wawo. 



Qy*j>j*** ( -^' *t» 



<^$j$$$&$3& 



e^msk&&#s 









9 '9 <*Al ' t 






Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 I 1255 I Y ^ *> 



*\A |J^Jl 3jj-j 



35. Kodi tiwachite Asilamu 
monga ochimwa. 

36. Kodi nchiyani chakupezani! 
Nanga mukuweruza bwanji 
(Maweruzo opanda 
chilungamowa)? 

37. Kapena muli ndi buku 
limene Mukuwerenga. 

38. Kuti mulinazo mmenemo 
zomwe Mukuzifiina. 

39. Kapena muli nawo 
mapangano ndi Ife okafika mpaka 
tsiku lomaliza Akuti inu 
mudzapeza zimene 
Mukudziweruzira? 

40. Afunse (iwe Mtumiki) 
Ndani mwa iwo amene ali 
mtsogoleri (Pa malamulo 
amenewa)? 

41. Kapena iwo ali nawo 
othandidzana nawo (Pa mau awa)? 
Ndipo atabweretsa Othandizana 
nawo ngati akunena zowona! 

42. (Akumbukire) tsiku la 
mavuto Okhwima, ndipo 
adzaitanidwa (akafiri) kuti Achite 
sijida (polambira Chauta) koma 
Sadzatha. 

43. Maso awo adzangoti pansi 
zyoli, Manyazi ndi kunyozeka 
Kudzawaphimba; kumachita kuti 
adali Kuitanidwa (padziko lapansi) 



*u^3£2\&& 



"&*''?■», 






j&* a 






««^(^ 






Surat 68. Al-Qalam Juzu 29 



1256 



t* frj*-i 



*\A ^JLoJl ojj** 



kuti Agwetse nkhope pansi pomwe 
iwo Adali ndi moyo wa ngwiro 
(Koma ankakana). 

44. Ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi 
amene Akukanira nkhani iyi 
tiwakokera Kuchilango 
pang'onopang'ono Pamene iwo 
sakudziwa (mmene chiti 
Chiwadzere chilangochi) 

45. Ndipo ndikuwalekerera 
(pochedwetsa Chilango); ndithudi 
makonzedwe Anga Ngokhwima, 
(palibe angapulumuke Mmenemo). 

46. Kapena ukuwapempha 
malipiro (Pofikitsa uthenga) kotero 
kuti iwo Akulemedwa ndi 
kulipira? 

47. Kapena ali nazo (nzeru) 
zobisika Kotero kuti iwo akulemba 
(zimene Akuweruzazo)! 

48. Choncho pirira ndi lamulo 
la Mbuye wako (Chifukwa 
chowalekerera ndi Kuchedwetsa 
chipulumutso chako); ndipo 
Usakhale ngati mwini nsomba 
(Yunusu pa changu ndi mkwiyo 
kwa Anthu ake) pamene adaitana 
(Mbuye wake) uku ali wodzazidwa 
ndi Mkwiyo (kupempha kuti 
chidze Mwachangu chilango kwa 
anthu ake). 

49. Chikadapanda kumfikira 
chisomo Chochokera kwa Mbuye 



©££U 



<%&&%$& Q& 






®, 



u 



%3&&4@fi*& 



'f »tev1' tv '&\* > 






M lpttf^**^S^ 33$ 



Siirat 68, Al-Qalam Juzu 29 1257 t * *j*-i 



nA fJUft 5^ 



wake (ndi Kuvomera kulapa 
kwake), Akadaponyedwa 
(kuchokera m'mimba Mwa 
chinsomba chija) pagombe 
(Popanda kanthu) ali 
wodzudzulidwa 

50. Koma adamsankha Mbuye 
wake (Povomera kulapa kwake) 
ndipo Adamchita kukhala mmodzi 
wa anthu Abwino. 

51. Ndithudi anthu amene 
sadakhulupirire Adayandikira 
kukutereretsa ndi Kunyogodola 
kwa maso awo (chifukwa 
Chachidani ndi mkwiyo) pamene 
Adamva chikumbutso(Qur'an), 
ndipo Akunena kuti iyeyo 
ngwamisala. 

52. Ndipo ichi sichina, koma 
(ndi phunziro, Ndi nzeru) ndi 
chikumbutso kwa Zolengedwa 
zonse. 






®G^\&4^%^ 






9$^iWZ 




Surat 69. Al-Haqqah Juzu 29 



1258 



r* *>» 



*\ ^ aSU-I 3j^-> 




Sura yolemekezekayi, yasonyeza mmene zinthu zidzakhalire 
tsiku la chimaliziro (Kiyama) ndipo yafotokoza zimene 
zidawapeza anthu akale monga kuonongeka ndi chilango 
champhamvu pamene adatsutsa uthenga wa Mulungu. 

Yafotokozanso za kuombedwa lipenga losonyeza kutha kwa 
dziko ndi zimene zidzaonekera nthaka, mapiri ndi thambo 
monga kusintha ndi kuchoka; ndi zimene zidzachitika 
motsagana ndi zimenezo monga anthu kuonekera kwa Mulungu 
ndi kuweruzidwa pa zomwe adachita. 

Surayi yapereka uthenga wabwino kwa anthu akudzanja 
iamanja, ochita zabwino, kuti adzakumana ndi malipiro abwino; 
umene udzakhala mtendere wamuyaya. Ndipo yawachenjeza 
anthu akumanzere, ochita zoipa, kuti adzakumana ndi chilango 
chowawa. 

Ndipo Surayi yamaliza ndi kunena zachoonadi cha uthenga 
wa Muhammad (SAW) umene adaufikitsa kwa anthu, ndi 
choonadi cha Qur'an yomwe ili choonadi chochokera kwa 
Mulungu. 




Siirat 69. Al-Haqqah Juzu 29 1259 r <\ *>» 



i ^ aiu-i Sjj-- 



Surat Al-Haqqah LXIX 



:**-' 


L-\_ £ 


- 4§^ -v 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Chakudza cha choonadi 
(chomwe ndi Kiyama). 

2. Kodi chakudza cha choonadi 
nchiyani? 

3. Nanga nchiyani 
chikudziwitse za chakudza Cha 
choonadicho? 

4. Asamudu ndi a Adi adatsutsa 
Zakudza kwa Kiyama (yomwe 
Idzadzidzimutsa zolengedwa 
Mwamphamvu ndi zoopsa zake). 

5. Tsono Asamudu 
adaonongedwa ndi Phokoso 
lopyola muyeso, (Lamphamvu 
kwambiri). 

6. Ndipo Adi adaonongedwa 
ndi Chimphepo cha mkutho, 
chozizira, (Champhamvu 
kwambiri). 

7. Mulungu adaachitumiza kwa 
iwo pa Usiku usanu ndi uwiri ndi 
masana asanu Ndi atatu 
mosadukiza; kotero Ukadawaona 
ali lambalamba mmenemo Ngati 
mathunthu a mitengo ya kanjedza 
Yopanda kanthu m'kati mwake. 

8. Kodi nanga ukumuona 
wotsala mwa Iwo? 



o^l^jM^U- 



^ 



m%\ 



©fcait 



©\3xa1u5Ljae5 



<^$ffixjt>&$ 



(s ^\ i \^'&%& 



hi^^^^%^ 






*&%&»&& 



Surat 69. AI-Haqqah Juzu 29 



1260 



r* >>i 



"\ ^ 43li-1 5jj-» 



9. Ndipo Firiaun ndi amene 
adalipo iye Asadabadwe, ndi 
khamu la anthu amidzi 
Yotembenuzidwa (anthu a Luti) 
adadza Ndi machimo (akulu). 

10. Ndipo (yense wa iwowa) 
adanyoza Mtumiki wa Mbuye 
wawo; choncho Adawalanga 
chilango chopitirira muyeso. 

11. Ndithu pamene madzi 
adasefukira Mopyola muyeso 
(mpaka kumeza Mapiri nthawi ya 
chigumula cha Nowa) Ife 
tidakukwezani mchombo 
choyandama Ndi kuyenda. 

12. Kuti tichichite 
(chochitikacho chomwe 
Okhulupirira adapulumuka nacho; 
Osakhulupirira adaonongeka 
nacho) Kukhala lingaliro ndi 
phunziro kwa inu, Ndikuti lisunge 
(nkhaniyi) khutu losunga. 

13. Likadzaimbidwa lipenga, 
kuimba Kumodzi kokha (zamoyo 
zonse zidzafa), 

14. Ndipo nthaka ndi mapiri 
nkuchotsedwa M'malo mwake ndi 
kuphwanyidwa Kamodzi kokha. 

15. Tsiku limenelo, chakudza 
Chidzakhala kuti chadza (imene ili 
Kiyama). 

16. Ndipo thambo lidzasweka 
choncho ilo Tsiku limenelo 






§>&*"* 












^^2S#teM2£ 



Surat 69. Al-Haqqah Juzu 29 1261 I * * *& 



i ^ du-i o 



d jj-- 



lidzakhala lofooka (Pamene lidali 
lolimba). 

17. Ndipo Angelo adzakhala 
m'mphepete Mwake, ndipo 
pamwamba pawo Tsiku limenero 
(Angelo) asanu Ndi atatu 
adzasenza mpando wa Mbuye wako. 

18. Tsiku limenelo 
mudzabweretsedwa Kuchiweruzo;) 
sichidzabisika chilichonse 
Chobisika mwa inu. 

19. Tsono amene adzapatsidwa 
kaundula Wake chakudzanja 
lakumanja kwake Adzanena 
(mokondwa kwa amene ali 
M'phepete mwake): "Tengani! 
Werengani kaundula wanga!" 

20. Ndithudi ine ndidatsimikiza 
(padziko Lapansi) kuti 
ndidzakumana ndi Chiwerengero 
changa. 

21. Choncho, iye adzakhala mu 
moyo Wosangalatsa 

22. M'munda wapamwamba. 

23. Zipatso zake zoyandikira 
pansi (zosavuta Kuzithyola) 

24. (Adzawauza kuti:) "Idyani, 
ndipo imwani Mosangalala pa 
zimene mudatsogoza Mmasiku aja 
adapita (apadziko lapansi). 

25. Ndipo amene adzapatsidwe 
kaundula Wake kudzanja lake 



^t>>ws^uacK 



«2$fc3U® 



«£_? ViStf .<*■*'»* 









&&*&$&&'& 






Surat 69. Al-Haqqah Juzu 29 1262 I * * *>» 



t H tflJ-l 5jj-» 



lamanzere, Adzanena 
(modandaula): "Kalanga ine! 
Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa 
Kaundula wangayu! 

26. Nkusadziwa chiwerengero 
changa! 

27. Ha! imfa ija 
ikadandimaliziratu (Ndi 
kundilekanitsa ine ndi zimenezi). 

28. Chuma changa 
sichidandithandize ! 

29. Mphamvu zanga (ndi moyo 
wanga Wathanzi) zandichokera!" 

30. (Kudzanenedwa kwa angelo 
Oyang'anira Jahena): Mgwireni 
ndipo Mnjateni (pomphatikiza 
manja ndi Khosi)! 

31. Kenako mponyeni kumoto. 

32. Kenakonso mlowetseni 
mtcheni lotalika Mikwamba 
makumi Asanu ndi awiri! 

33. Ndithudi, iye sadali 
Kukhulupirira mwa Mulungu 
wamkulu. 

34. Sadalinso kulimbikitsa 
Zodyetsa osauka. 

35. Basi, lero kuno Alibe 
bwenzi (lomthandiza). 

36. Ndipo alibe chakudya 
kupatula Mafinya (a anthu 
akumoto) 



®^^ics^c$& 



©^*(JWfc 
v*i>2 Uj*4-- V^eja jO-J- Jt,>> 



tS&K&fr* 1 "« 



h$frfr.%%\3L& 



Surat 69. AI-Haqqah Juzu 29 I 1263 I Y ^ *>i 



*\ ^ AdU-l 5jj-a 



37. Zomwe palibe angazidye 
kupatula Ochimwa (mwadala). 

38. Choncho ndikulumbirira 
zimene Mukuziona, 

39. Ndi zimene simukuziona. 

40. Ndithudi iyi (Qur'an) 
ndiliwu la Wamthenga 
wolemekezeka (Jibril). 

41. Ndipo simawu a mlakatuli 
Ndi zochepa zimene 
Mukuzikhulupirira. 

42. Ndiponso simawu A mlosi; 
ndi zochepa Zimene 
mumalangizika nazo! 

43. (Ichi ndi) chivumbulutso 
Chochokera kwa Mbuye wa 
zolengedwa. 

44. Ndipo (Mneneri) 
akadatipekera Bodza lililonse. 

45. Tikadamgwira 
mwamphamvu, 

46. Ndipo tikadadula mwa iye 
mtsempha Wamoyo (kotero kuti 
ndikuferatu Nthawi yomweyo), 

47. Sipakadapezeka aliyense 
mwa inu Womteteza (kuchilango 
Chathu). 

48. Ndithu, iyi (Qur'an) ndi 
phunziro Labwino kwa owopa 
(Mulungu.) 






©J 






'% 






®m%&®> 



Siirat 69. Al-Haqqah Juzu 29 1264 * * *j*-i 



n ^ 4dU-i ojj-- 



49. Ndithu Ife, tikudziwa kuti 
ena mwa inu Atsutsa (Qur'an) 

50. Ndipo ndithu, iyi (Qur'an) 
idzakhala Chowadandaulitsa 
(chachikulu) Osakhulupirira 
(pamene adzaona Chilango chawo 
ndi mtendere wa Okhulupirira). 

51. Ndithu, iyoyi ndi choonadi 
Chotsimikizika; (mulibe chikaiko), 

52. Basi, lemekeza dzina la 
Mbuye wako Wamkulu (Pitiriza 
kutamanda dzina Lake). 






®yg\&ttii 



i^OpA^* 




Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 1265 * * *>» 



V * jr jt*^ «j>-» 




M'surayi muli zoopseza za tsiku la Kiyama ndikuti 
lidzakhala lalitali kwambiri pamodzi ndi zoopsa zazikuluzikulu. 
Ndi kuti tsiku limenelo munthu adzayesa kupereka dipo la ana, 
mkazi wake, m'bale wake makolo ake ndi zonse za m'dziko kuti 
apulumuke kuchilango chamoto, koma zonsezo 
sizidzavomerezedwa. 

Surayi yalongosolanso kuti munthu ngofooka kwambiri pa 
nthawi yamavuto ndi nthawi yopeza bwino, kupatula amene 
Mulungu wawateteza kukhalidwe loipa pakulimbikitsa mitima 
yawo kuopa Mulungu yekha ndi kugwira ntchito yabwino, 
osatekeseka ndi chilichonse ngakhale chiopse chotani. 




Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 | 1266 | * ^ *jk-\ V » £J uH o^ 



Surat Al-Ma'arijLXX 









M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Wopempha adapempha kuti 
chiwadzere Msanga chilango 
chopezekacho, (M'kupempha kwa 
chipongwe ndi Kotsutsa) 

2. Kwa okanira palibe 
Angachitsekereze, 

3. Chochokera kwa Mulungu 
Mwini Makwerero. 

4. Angelo ndi Jiburil amakwera 
kwa lye (Mulungu) m'tsiku 
Lomwe kutalika kwake kuli ngati 
zaka Zikwi makumi asanu (50 000). 

5. Choncho, pirira (iwe 
Mtumiki{SAW} Kupirira 
kwabwino, 

6. Ndithu, iwo akuona (tsiku) la 
Kiyama kuti palibe; silingachitike. 

7. Koma Ife tikuona kuti 
ndilochitika. 

8. Tsiku limene thambo 
lidzakhala Ngati mtovu 
wosungunuka. 

9. Ndipo mapiri adzakhala ngati 
ubweya (Wongouluka wokha). 

10. Ndipo m'bale sadzafunsa Za 
m'bale wake, 



Q^lfc^JJl^ 



-£ 






Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 1267 * * >> 



V* ?r jUil 3 



£j mn fljj^ 



11. Ngakhale adzawalole kuti 
aonane Ndi kudziwana pakati 
pawo (Sadzafunsana).Wochimwa 
adzalakalaka Kuti 
akadaziwombola ku chilango cha 
Tsiku limenelo ndi ana ake, 

12. Ndi mkazi wake, ndi m'bale 
wake, 

13. Ndi akurntundu wake amene 
Amamsunga. 

14. Ndi (kulipira) zonse Za 
m'dziko, kuti Zimpulumutse. 

15. Iyayi, (siya iwe wamachimo 
zimene Ukulakalakazo)! Ndithu 
umenewu ndi Moto wa malawi. 

16. Wosupula mwamphamvu 
khungu, 

17. Udzaitana (potchula dzina la 
aliyense) Amene 

adachitembenuzira msana Choona 
ndi kunyoza; 

18. Adasonkhanitsa (chuma) 
ndi kusunga (M'nkhokwe zake 
popanda Kuperekera chopereka 
cha Mulungu) 

19. Ndithu, munthu 
walengedwa kukhala Wosapirira. 

20. Mavuto akamkhudza amada 
nkhawa. 

21. Koma zabwino 
zikamkhudza amamana (Ena ndi 
kuiwala mavuto amene adali Nawo). 















&is<sws& 






Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 1268 * * *> 



V • £jt*il 5jj-» 



22. Kupatula opemphera, (iwo 
alibe mbiri Zoipazi). 

23. Iwo amene akupitiriza 
mapemphero Awo; (sakuwaleka 
ngakhale zivute Chotani). 

24. Ndi amene mchuma chawo 
muli Gawo lodziwika, 

25. La wopempha ndi 
wosapempha. 

26. Ndi amene akuvomereza za 
tsiku La malipiro (ndi 
kumalikonzekera.) 

27. Ndi iwo amene akuopa 
chilango Chochokera kwa Mbuye 
wawo, 

28. Ndithu, chilango cha Mbuye 
wawo Nchosapulumuka nacho 
(munthu Woipa). 

29. Ndiponso iwo amene 
akusunga Umaliseche wawo 
(posachita Chiwerewere), 

30. Kupatula kwa akazi awo ndi 
Amene manja awo akumanja 
apeza; Ndithu, pazimenezo iwo 
Sangadzudzulidwe. 

31. Koma amene angafune 
(zina) Kusiya zimenezi iwowo 
ndiwo Olumpha malire. 

32. Ndi iwo amene amasunga 
mwaubwino Zimene 
amasungisidwa ndi zimene 
alonjeza. 



'&" ! 



tft 






9 m' [<''*W9J> *9 •til' 






Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 [ 1269 | * * *& V * g- jUlt *^ 



33. Ndi iwo amene amaima 
molungama Popereka umboni 
wawo. 

34. Ndiponso iwo amene 
amasunga (Mwaubwino) 
mapemphero awo. 

35. Amene ali ndi mbiri 
zimenezi adzakhala M'minda 
(yamtendere) ali Olemekezedwa. 

36. Kodi kuli chiyani kwa 
amene akana (Chikhulupiriro) 
akuthamangira kwa iwe (Maso ali 
pamtunda)? 

37. Atakuzungulira ena 
chakumanja ena Chakumanzere 
atazungulira. 

38. Kodi akulakalaka aliyense 
mwa iwo Kuti akalowetsedwe ku 
munda Wamtendere? 

39. Asiye (kukhumba kwawo 
kokalowa ku Munda wa 
mtendere)! Ndithu Ife 
Tidawalenga kuchokera m'zimene 
Akudziwa! (madzi opanda pake). 

40. Ndikulumbirira Mbuye wa 
kuvuma ndi Kuzambwe konse 
ndithu Ndife Wokhoza. 

41. Kuwasintha ndi kudzetsa 
abwino Kuposa iwo; Ife palibe 
(chilichonse) Chotipambana. 

42. Asiye azingolankhula 
zopanda pake ndi Kumangosewera 






S?\i SS 9 S* t S 



®wG& ti^lfc^gM tf 






*j& &&<&!*$% 



$ayaty 









Surat 70. Al-Ma'arij Juzu 29 | 1270 | Y^ *£\ V * ^jUli Sjj- 



mpaka adzakumane Ndi tsiku lawo 
limene Akulonjezedwa. 

43. Tsiku limene adzatuluke 
m'manda Uku akuthamanga 
(kudza kwa woitana) Ngati kuti 
akuthamangira kumafano awo 
(amene adali Kuwapembedza). 

44. Maso awo ali zyoli,(osatha 
kuwakweza); Kuyaluka 
kutawaphimba! Limenelo Ndilo 
tsiku lomwe adali kulonjezedwa 
(Pomwe adali padziko lapansi. 






&\ty%^gffify?> 



^SlyW^ 




Surat 71. Nuh 



Juzu 29 I 1271 T * *j*-i 



v y ^y 5 j^ 




SURAT NUH LXXI 




Surayi yafotokoza mwatsatanetsatane nkhani ya Nuhu (AS) 
pamodzi ndi anthu ake. Ndipo yafotokozanso za kuitana kwake 
kwa anthu ake molimbika, kenako mobisa, ndipo kenakonso 
molimbika. Ndiponso yalongosola kusuma kwake kwa Mulungu 
za kusalabadira kwawo ndi makani awo. Yanenanso za 
kupitiriza kwawo kugwadira mafano mpaka adayenera kulandira 
chilango cha Mulungu. 

Pamene Nuhi adataya mtima pazakuvomera kwawo 
pakuitana kwake, adapempha Mulungu kuti awaononge onse ndi 
kuwathetsa. 

Kenaka adadzipemphera yekha kudzanso makolo ake, 
okhulupirira aamuna ndi aakazi, kuti Chauta awakhululukire. 




Surat 71. Nuh 



Juzu 29 



1272 



r^ *>i 



v^ 



C>'.» < 



Surat NuhLXXI 



m 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndithu Ife tidamtuma Nuhu 
kwa Anthu ake, (ndikumuuza 
kuti): "Chenjeza anthu ako 
chisadawafike Chilango 
chowawa." 

2. Adanena (Nuhu), "E, inu 
anthu anga! Ndithu, ine 
ndimchenjezi kwa inu Woonekera 
poyera (wolongosola za Uthenga 
wa Mbuye wanu M'chiyankhulo 
chimene mukuchidziwa). 

3. Mpembedzeni Mulungu 
ndipo muopeni Ndikutinso 
mundimvere (Pazimene 
ndikukulangizani). 

4. (Ngati mutero) 
adzakukhululukirani Machimo anu 
ndi kukutalikitsirani moyo Wanu 
kufikira m'nthawi imene yaikidwa 
(Kuti ndiwo malire akutalika kwa 
Moyo). Ndithu nthawi ya Mulungu 
Ikabwera siyichedwetsedwa 
(Ngakhale pang'ono). 
Mukadakhala Mukudziwa. 

5. Adanena (Nuhu): "Ambuye! 
Ine Ndaitanira anthu anga 
(Kuchikhulupiriro) usiku ndi usana 
(Popanda kufooka). 



§yi^ £ .; *■$£:>■ 



o^t^jii^u- 



-a 






®y£kVji&\j&\\j!&\y\ 






t\ 9 '\ >* 9 i 9 *" 9 \l,» ' 



©Ij^iJ 



Surat 71. Nuh 



Juzu 29 



1273 ™*j*-» 



V> 



C> 5 J>" 



6. Kuitana kwanga 
Sikudaonjezere (chilichonse) koma 
Kuthawa basi (kuchikhulupiriro 
Chanu). 

7. Ndipo ine nthawi iliyonse 
ndikawaitanira (Ku chikhulupiriro 
Chanu) kuti Mwakhululukire, 
akuika zala zawo M'makutu 
mwawo (kuti asamve Uthenga 
Wanu), ndipo akudziphimba Ndi 
nsalu zawo (kuti asaone nkhope 
Yanga), ndipo akupitiriza kukana 
Kwawo ndi kudzikweza kwakukulu. 

8. Kenaka ine ndawaitanira 
(kwa Inu) Ndi mawu ofuula, 

9. Kenakanso (ine 
ndawaitanira) Molengeza poyera 
ndiponso Mwachinsinsi mobisa. 

10. Choncho ndidati (kwa anthu 
anga): Pemphani kwa Mbuye wanu 
chikhululuko (Pa kukana kwanu 
ndi kutonza kwanu): Ndithu, lye 
sadasiye kukhala Wokhululukira 
(machimo kwa amene Akubwerera 
kwa lye). 

11. Akutumizirani mvula 
yotsika Mochuluka, 

12. Ndikukupatsani chuma ndi 
ana, (Zomwe ndi zokongoletsa za 
dziko Lapansi), ndi kukupangirani 
minda (Yokongola) ndi 
kukupangirani mitsinje (Yothirira 
mbewu zanu ndi kumwetsa Ziweto 
zanu). 



<m3m^kkfc 












Surat 71. Nuh 



Juzu 29 



1274 



Y<\ ftjJb-i 



V ^ c y 5 j^ 



13. Kodi chifukwa ninji 
simupereka Ulemu kwa Mulungu 
(woyenera Umulungu Wake kuti 
akakuchitireni Chifundo ndi 
kukupulumutsani ku Chilango), 

14. Pomwe lye adakulengani 
Mnjira zosiyanasiyana: (Madzi a 
umunthu, kenako Magazi, kenako 
magazi Ochindikara, kenako 
Mafupa ndipo kenako mnofu), 

15. Kodi simudaone momwe 
Mulungu Adalengera thambo 
zisanu ndi Ziwiri mosanjikizana? 

16. Ndi kuupanga mwezi 
mthambomo Kukhala kuunika, 
ndiponso Kulipanga dzuwa 
kukhala nyali. 

17. Ndipo Mulungu 
adakulengani Kuchokera m'nthaka 
monga mmera. 

18. Kenako adzakubwezerani 
Momwemo 

ndikudzakutulutsaninso (Popanda 
cholepheretsa). 

19. Ndipo Mulungu 
wakupangirani Nthaka kukhala 
ngati choyala, 

20. Kuti muziyendayenda 
m'menemo M'njira zazikulu." 

21. AdanenaNuhu: "Ambuye! 
Ndithu Anthu anga andinyoza 
(pazimene Ndawalamula kuti 



©B&A&S&tffc 



®\$\£\p&. 






t I " '9 ' 






^<®£j#*a6 






&\X£$titi£'&.i%>j£ 



o» 



Surat71.Nuh 



Juzu 29 



1275 



M *>i 



v^ 



C> i»* 



akhulupirire Inu ndi kupempha 
chikhululuko Chanu), ndipo 
(ofooka mwa iwo) Amtsatira 
yemwe chuma chake ndi ana Ake 
sizidzamuonjezera (chilichonse 
Chabwino) koma kutaika (ndi 
Kuonongeka patsiku lomaliza). 

22. Ndipo (eni chuma ndi ana) 
awatchera (Otsatira awo) ndale 
zazikulu (Ndi zopyola muyeso kuti 
Asakhulupirire)" 

23. Ndipo adanena (kwa otsatira 
awo): "Musasiye kupembedza 
milungu Yanu: Musamusiye 
Wadda, Suwaa, Yaghutha, Ya'uka 
ndi Nasra (Maina amafano awo)." 

24. Ndipo ndithu iwo asokeretsa 
(anthu) Ambiri; ndipo 
musawaonjezere ochita Zoipa 
(china chake) koma kusokera basi" 

25. Chifukwa cha zochimwa 
zawo Adamizidwa ndi 
kulowetsedwa kumoto (Waukulu 
woyaka); sadapeze Owapulumutsa 
ndi kuwateteza m'malo Mwa 
Mulungu. 

26. Ndipo adanena Nuhu 
(atataya mtima Za anthu ake): 
"Ambuye! Musasiye Aliyense 
mwa osakhulupirira kukhala 
Padziko. 

27. Ndithu, Inu Ambuye ngati 
muwasiya (Popanda kuwaononga 



WX$fpiJ& 






*w^ 



'"■&m-. 









&UkW5fc«l$l 



Surat 71. Nuh 



Juzu 29 



1276 t**>i 



V 1 £> ijy* 



ndi kuwathetsa) Asokeretsa 
akapolo anu (kunjira Yolungama). 
Ndipo sangabereke (ana Abwino) 
koma oipa; osakhulupirira (Okhala 
kutali ndi choonadi, ndiponso 
Onyoza Inu). 

28, "Mbuye wanga! 
Ndikhululukireni ndi makolo 
Anga, ndi aliyense walowa 
M'nyumba yanga ali okhulupirira 
Ndi okhulupirira aamuna ndi 
okhulupirira Aakazi. Ndipo 
musawaonjezere anthu 
Achinyengo chinachake koma 
Kuwaononga basi." 



«6ttf iwfeasyssu 







Surat 72. A 1- Jinn Juzu 29 



1277 



t* *j*-1 



VY jA-iaj^- 




Mulungu walamula Mneneri wake (SAW) msurayi kuti 
adziwitse anthu zimene zavumbulutsidwa kwa lye zoti ziwanda 
zidamvera kuwerenga kwake kwa Qur'an ndipo zidavomereza 
uthenga wake. Ndiponso izo zidafotokoza mmene opulukira 
mwa iwo kudzanso abwino awo, adalili. Ndi kuti zinkakhala 
m'malo okhala nkumamvera nkhani za kumwamba mobera. 
Koma tsopano akuzipirikitsa. 

Ma aya a surayi asonyeza njira za Chisilamu kwa olungama 
ndi osalungama. Ndipo afotokoza kuti mapemphero ndi misikiti 
zikhale za Mulungu yekha. Ndiponso yafotokoza zoti ziwanda 
zidamzinga Mtumiki Muhammad(SAW) kumverera Qur'an 
yomwe adali kuwerenga. 

Surayi yafotokozanso kuti pali zina zimene Mtumiki (SAW) 
angazithe ndipo pali zina zimene sangazithe. Ndipo 
yachenjezanso onyoza Mulungu ndi Mtumiki Wake kuti 
akalowa kumoto. Pomaliza yanenetsa kuti Mulungu yekha ndiye 
akudziwa. 




Surat 72. Al-Jinn Juzu 29 1278 * * *>» 



vr jfclSjj- 



Surat Al-Jinn LXXII 



*§u ^*^ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nena (iwe Mtumiki(SAW), 
kwaanthu Ako): 

"Kwavumbulutsidwa kwa Ine kuti 
gulu la ziwanda lidamvetsera 
(Kuwerenga kwanga Qur'an) 
ndipo Lidanena (kumtundu wawo), 
ndithu, Tamvetsera Qur'an 
yodabwitsa, (Sitidaimve yonga iyi 
chiyambire). 

2. Ikuitanira kuchilungamo, 
ndipo Taikhulupirira. Ndipo 
sitimphatikiza Aliyense ndi Mbuye 
wathu, (pa Mapemphero.) 

3. Ndipo ndithu, ukulu ndi 
ulemerero wa Mbuye wathu 
watukuka; Sadadzipangire mkazi 
kapena mwana. 

4. Ndipo ndithu, mbuli za mwa 
ife zakhala Zikunenera Mulungu 
mawu abodza (Okhala kutali ndi 
choonadi). 

5. Ndipo ndithu ife tinkaganiza 
kuti Anthu ndi ziwanda 
sangamnenere Mulungu zabodza 
(zosayenera Ulemerero Wake). 

6. Ndipo ndithu, padali amuna 
amuwanthu Amapempha chitetezo 
kwa amuna Amziwanda, ndipo 



o^l^JII^L, 



— Z& 






:\ '* 






i^H3M%&$$m 



y k * 'f ' /i ' 






Siirat 72. Al-Jinn Juzu 29 



1279 



Y<\ *>» 



VY^lSj^- 



adawaonjezera (Amuna 
amziwanda) kupitiriza Machimo 
awo, kupulukira (ndi Kuchenjerera 
anthu.) 

7. Ndipo iwo amaganiza monga 
momwe Mumaganizira inu kuti 
Mulungu Sadzaukitsa aliyense 
(atafa). 

8. Ndithu, ife tidafuna kukafika 
Kumwamba; tidakupeza kutadzala 
Alonda (Angelo) amphamvu ndi 
Zenje zamoto. 

9. Ndithu ife tidali kukhala 
m'menemo (Kale) mokhala 
momvetsera; (mobera Nkhani 
zakumwamba). Koma amene 
Afune kumvetsera tsopano apeza 
chenje Chamoto chikudikirira (kuti 
chimgwere lye ndi kumuononga). 

10. Ndithu, ife sitikudziwa 
chilango Chimene akuwafunira 
am'dziko (Polondera kumwamba, 
kuletsa Kumvetsera nkhani 
zakumeneko); Kapena Mbuye 
wawo akuwafunira Zabwino ndi 
chilungamo (pazimenezo). 

11. Ndithu, ena mwaife ndi 
abwino Koma ena sali 
choncho.Tili njira Zosiyanasiyana. 

12. Ndithu ife tidadziwa kuti 
Mulungu Sitingathe kumlepheretsa 
(lamulo Lake Pa ife paliponse 
tingakhale) padziko Lapansi, ndipo 



©tou>3 









Surat 72. Al-Jinn Juzu 29 



1280 



^ *>i 



Vt^lo^j^ 



sitingamlepheretsenso Pomzemba 
ndi kuthawira (kumwamba) 

13. "Ndipo ife pamene tachimva 
chiongoko (Qur'an) tachikhulupirira 
ndipo amene ati Akhulupirire mwa 
Mbuye wake saopa 
Kumchepetsera (chabwino kapena 
Kumuonjezera machimo ake). 

14. Ndithu, mwa ife alipo 
Asilamu Ndiponso mwa ife alipo 
opatuka (Munjira ya chilungamo); 
amene Walowa m'Chisilamu, 
iwowo ndi Amene alunjika njira ya 
choonadi. 

15. Koma opatuka (kunjira ya 
Chilungamo) adzakhala nkhuni za 
Jahannama." 

16. Ndithu, (anthu ndi ziwanda) 
Akadalungama panjira Ya 
chilungamo Tikadawamwetsa 
madzi ambiri (Okwanira nyengo 
zonse), 

17. Kuti tiwayese ndi zimenezo 
(mmene Angamyamikire Mulungu 
pa mtendere Wake pa iwo). Koma 
amene anyozera Kupembedza 
Mbuye wake, amlowetsa 
Kuchilango chovuta (chimene 
Sangathe kupirira nacho). 

18. Ndithu,misikiti ndi ya 
Mulungu yekha! Choncho, 
musapembedze aliyense Pamodzi 
ndi Mulungu. 















MP&&te^*3\m 






Surat 72. Al-Jinn Juzu 29 



1281 "*>» 



vr jjfc-i *>>. 



19. Ndipo ndithu, pamene 
adaima kapolo Wa Mulungu 
(Muhammad{SAW}, pa Swala 
yake) uku akumpembedza 
(Mulungu), ziwanda zidatsala 
pang'ono Kumgwera (chifukwa 
cha kuchuluka Kwawo ndi 
kumzinga podabwa ndi Zimene 
adaziona ndi kuzimva). 

20. Nena:"Ndikumpembedza 
Mbuye wanga M'modzi (Yekha) 
ndipo Sindingamphatikize ndi 
aliyense (M'mapemphero Ake)." 

21. Nena: "Ine ndilibe udindo 
wokupatsani Mavuto kapena 
chilungamo (Ndi zabwino)." 

22. Nena: "Ine palibe 
anganditeteze Kuchilango cha 
Mulungu (ngati Nditamnyoza) 
sindingapeze malo (Othawira 
kuchilango Chake) Kupatula kwa 
lye. 

23. Koma mphamvu imene ndili 
nayo Ndikufikitsa uthenga wa 
Mulungu umene 
Adanditumizira;ndithu amene 
anyoza Mulungu ndi Mtumiki 
Wake (ndi Kupatuka pa 
chipembedzo cha (Mulungu) 
Ndithu, moto wa Jahannama ndi 
Wake akakhala m'menemo 
Muyaya. 

24. Mpaka pomwe adzaziona 
zimene Alonjezedwa ndipamene 






^MSi^Gfe^a* 



©lo>| 



©i«USJ!W^9<8# 









Surat 72. Al-Jinn Juzu 29 



1282 



Y* *j*-l 



VY Jr\ Sjj- 



adzadziwa (Kuti) kodi ndani 
mwini mthandizi Wofooka 
ndiponso wochepekedwa 
Kuchuluka (kwa omtsatira, iwo 
kapena Asilamu)." 

25. Nena (kuti): "Sindikudziwa 
ngati Zomwe mukulonjezedwa (za 
chilango) Zili pafupi, kapena 
Mbuye wanga Azitalikitsa. 

26. (lye) ndi Wodziwa 
zobisika; Sazionetsa zobisika Zake 
kwa Aliyense (mzolengedwa Zake), 

27. Kupatula Mtumiki (Wake) 
amene Wamuyanja; (iyeyo 
amamdziwitsa Zobisikazo) ndipo 
ndithu amamuikira Alonda 
kutsogolo kwake ndi Kumbuyo 
kwake (omulonda). 

28. Kuti adziwe ngati afikitsa 
Uthenga wa Mbuye wawo, ndipo 
Wawazungulira (podziwa zonse 
Zili kwa iwo) ndipo wadziwa 
Kuchuluka kwa zinthu zonse 
Zimene zilipo; (palibe chobisika 
Kwa lye)." 






feWwo^Sf &&%2J»p* 






t L? 'f 

©bU*> 




Surat 73. Al-Muzzammil Juzu 29 



1283 



r* *>i 



vr jjijii Sj^ 




SURAT AL-MUZZAMMIL LXXIII ^ * 




M'surayi Mulungu akulamula Mneneri Wake (SAW) kuti 
aziima gawo lalikulu la usiku kupemphera ndi kuwerenga 
Qur'an mofatsirira. 

lye ndi gulu la omtsatira ake, adaima kupemphera potsatira 
lamuloli. Koma kenako Mulungu adawapeputsira powalamula 
kuti azipemphera Swala zisanu ndi kupereka zakati ndi sadaka, 
ndiponso ndi kuchulukitsa kupempha chikhululuko Chake. 

Adamlamulanso kupirira pazimene akumuyankhulira otsutsa 
pomuuza kuti amsiire Mulungu, lye ndiye amene adziwe 
chochita nawo. 

Osakhulupirira aopsezedwa m'surayi powauza kuti awalanga 
ndi chilango choopsa monga chomwe adalangidwa nacho anthu 
akale amene adali kunyoza Mneneri wa Mulungu. Ndipo 
aopsezedwanso ndi zoopsa zina zomwe zidzachitika tsiku 
lomaliza. 




Surat73.Al-MuzzammilJuzu29 1284 t ^ *j*-t 



vr »i i iy * 



Surat Al-Muzzammil LXXIII 



; 



M&ffiv 



3^ 



=£=, ,_ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ee, iwe wadziphimba (ndi 
nsalu!) 

2. Imirira usiku (upemphere), 
Kupatula nthawi yochepa. 

3. Theka lake kapena chepetsa 
thekalo Pang'ono (mpaka ufike 
chimodzi Mwazigawo zitatu za 
usiku). 

4. Kapena wonjezapo (mpaka 
ufike zigawo Ziwiri mwa zigawo 
zitatu za usiku;) Ndipo werenga 
Qur'an mofatsa (Lemba ndi 
lemba). 

5. Ife tikuvumbulutsira iwe 
(Mneneri) Mawu olemera (yomwe 
ndi Qur'an). 

6. Ndithu, kudzuka usiku Ndi 
kuchita mapemphero 
Kumalowerera (mumtima) 
Kwambiri, ndipo zoyankhula Zake 
zimakhala zoongoka ndi Zolunjika 
bwino (kuposa Mapemphero 
amasana). 

7. Ndithu, masana uli ndi 
Zochitachita zambiri; 
(Umatanganidwa ndi ntchito 
Yauthenga; dzipatse danga Usiku 
polimbika kupemphera). 



OJ&&\i£&\&\j 



-^ 






mm 



©^>'lU^^ia^& 



Surat 73. Al-Muzzammil Juzu 29 1285 * * *>> 



vr » o^j- 



8. Ndipo tchula dzina la Mbuye 
wako (Amene adalenga ndi kulera 
zinthu), Ndipo udzipereke 
kwathunthu kwa lye. 

9. (lye ndiye) Mbuye wa 
kuvuma ndi Kuzambwe; palibe 
wopembedzedwa Mwachoonadi 
koma lye. Mchiteni Kukhala 
mtetezi (warm pazinthu Zanu 
zonse). 

10. Ndipo pirira pa zimene 
akunena. Ndipo apewe (ndi mtima 
wako); Kupewa kwabwino. 

11. Ndisiye Ine ndi otsutsa eni 
Kupeza bwino; ndipo alekerere 
Kanthawi kochepa. 

12. Ndithudi, tili ndi 
mitundumitundu Ya unyolo ndi 
moto Woyaka, 

13. Ndi chakudya chotsamwitsa 
Ndi chilango chowawa. 

14. Tsiku limene nthaka ndi 
mapiri Zidzagwedezeka; 
(kugwedezeka kwa Mphamvu 
kotero kuti) mapiri adzakhala 
Ngati mulu wa mchenga 
woyoyoka. 

15. Ndithu, Ife takutumizirani 
Mthenga Amene adzakhala mboni 
yanu (tsiku la Chimaliziro; monga 
momwe Tidamtumizira (Musa) 
kukhala Mtumiki kwa Firiauni. 









®%tf%sim& 






&&$&% 






Surat 73. Al-Muzzammil Juzu 29 



1286 



t* *jtr\ 



vr >jii Sj^ 



16. Koma Firiauni adamnyoza 
Mtumikiyo; Ndipo tidamulanga 
Chilango chokhwima. 

17. Kodi mungadzitchinjirize 
chotani ngati Mukana (chilango 
cha) tsiku (lomwe) Lidzachititsa 
ana kukhala ndi imvi? 

18. Thambo (pamodzi ndi 
mphamvu zake Ndi kukula 
kwake), lidzang'ambika (Tsiku 
limenelo) chifukwa cha kuopsa 
Kwa tsikulo, lonjezo la (Mulungu) 
Lidzakwaniritsidwa, (palibe 
wolipinga). 

19. Ndithudi, ma ay a awa 
(amene akunena Za kuwopsa kwa 
Kiyama) ndi Chikumbutso, 
choncho amene akufuna 
(Kuthandizika nawo) ayende 
panjira Ya Mbuye wake 
(pokwaniritsa Malamulo Ake ndi 
kuleka zoipa). 

20. Ndithu, Mbuye wako 
akudziwa kuti Iwe ukuima 
(kupemphera) Pafupifupi zigawo 
ziwiri mwa Zigawo zitatu za usiku 
kapena theka Lake, kape'nanso 
chigawo chimodzi mwa Zigawo 
zitatu za usiku, pamodzi ndi gulu 
La omwe uli nawo. Ndipo 
Mulungu NdiAmene amadziwa 
bwino muyeso Wa (nthawi za ) 
usiku ndi usana, Wadziwa kuti 
simungathe kuwerenga Zimenezo, 



©jk*** 









o*9' m Yy >.?4 9 9 S 9 ? frs ' 



Surat 73. Al-Muzzammil Juzu 29 



1287 



™ >>i 



vr »i s^ 



choncho wakukhululukirani. 
Werengani ndime imene yapepuka 
Yochokera m'Qur'an. Wadziwa 
kuti ena mwa inu adzakhala 
Odwala: (kudzawavuta kuimirira 
ndi Kuchezera usiku), ndipo ena 
adzakhala Akuyendayenda padziko 
(ndi cholinga Cha malonda ndi 
ntchito) kunka Nafunafuna ubwino 
wa Mulungu. Ndipo ena adzakhala 
akumenya Nkhondo panjira ya 
Mulungu (Ncholinga chotukula 
mawu Ake), Werengani chimene 
chapepuka chochokera mmenemo 
(m'Qur'an) ndipo Pitirizani 
kupemphera swala, perekani 
chopereka (chimene 
chakakamizidwa Kwa inu). Ndipo 
mkongozeni Mulungu Ngongole 
yabwino ndipo chilichonse 
chabwino chimene 
mwadzitsogozera mudzachipeza 
kwa Mulungu chili chabwino 
(kuposa zomwe mudazisiya 
m'mbuyo) ndi malipiro aakulu 
zedi ndipo mpempheni Mulungu 
chikhululuko (Pa uchimo wanu ndi 
chikhululuko pakunyozera kwanu 
kuchita zabwino). Ndithu, 
Mulungu Ngokhululuka 
Ngwachisoni. 






Surat 74. Al-Muddaththir Juzu 29 



1288 



r* *>i 



Vt yall 3j^ 




Surayi ikulamula Mneneri wa Chauta (SAW) kuti achenjeze 
anthu ake ndi kuti alemekeze Mulungu. Ndi kutinso asiye 
zosayenera kuchita ndi lye. Ndipo yafotokozanso za kuimbidwa 
kwa lipenga ndi kukhwima kwa chilango kwa okanira. 

Ikulamuliranso kuti am'siye wokana chisomo cha Mulungu 
yemwe amakhumba kuti awonjezeredwe zina popanda 
kuthokoza Mwini chisomo. Ndipo yafotokozanso mmene 
ankaganizira osakhulupirira Qur'an. 

Kenako Surayi yakumbutsa mitima kuti kalikonse kabwino 
ndi koipa kamene ikuchita, ndichikole cha mitimayo. Ndipo 
kenako yayankhula za anthu ambali ya kumanja mmene 
azikawafunsira mafunso anthu a kumoto owaliritsa nawo kuti: 
"Nchiyani chakulowetsani ku moto?" 

Surayi yamaliza ndi kufotokoza za ulemerero wa Qur'an 
ponena kuti umenewu ndi uthenga wabwino kwa amene 
akuulingalira, ndi kunenetsa kuti amene waulingalira uthenga 
umenewu akhala m'gulu la oopa Mulungu, amene adzapeza 
chikhululuko Chake. 




Surat74.Al-MuddaththirJuzu29 1289 T^tjJri 



Vt j>&\» iy * 



Surat Al-Muddaththir LXXIV 



m^w r 



jm& 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ee, iwe wadziphimba (nsalu)! 

2. Imirira ndipo uwachenjeze 
(Anthu za chilango cha Mulungu) 

3. Ndipo Mbuye wako (yekha) 
Umkulitse (pomulemekeza). 

4. Ndipo nsalu zako uziyeretse 
(Ndi madzi kuuve). 

5. Ndiponso zoipa (monga 
mafano Ndi zina zonse ) zipewe. 

6. Usapatse (anthu) ncholinga 
Choti ulandire zambiri. 

7. Chifukwa cha Mbuye Wako, 
pirira (kumalamulo Ake poleka 
Zomwe waletsa ndi kuchita zimene 
Walamula). 

8. Likadzaimbidwa lipenga, 

9. Tsiku limenelo lidzakhala 
Tsiku lovuta. 

10. Kwa osakhulupirira, 
silidzakhala Lofewa. 

11. Ndisiye ndiamene 
Ndidamlenga Ndekha, 

12. Ndipo ndampatsa chuma 
chambiri. 

13. Ndi ana okhala nawo 
(paliponse). 



o^JJt^Jtt^ 



^ 



Sao® 



&y&A*r 



(?£jb3&Qj 












©t^^ycJj 



Surat 74. AUVluddaththir Juzu 29 1290 t H *>t 



Vi yjdiSj^ 



14. Ndipo ndamkonzera 
(ulemerero), Kumkonzera 
(kwabwino). 

15. Kenako ali ndi dyera kuti 
Ndimuonjezere (zina popanda 
Kuthokoza). 

16. Koma sichoncho! Ndithu, 
iye Adali kutsutsa Zizindikiro 
Zathu. 

17. Ndidzamkakamiza 
kuchilango Chovuta: (kukwera 
phiri lakumoto Limene sakatha 
kulikwera). 

18. Iye adalingalira (mumtima 
Mwake) ndi kukonza bwino 
(Chonena chonyoza Qur'an); 

19. Choncho waonongeka! 
Adakonza bwanji (Poinyoza 
Qur'an)! 

20. Ndiponso 
waonongeka! Adakonza bwanji 
(Poinyoza Qur'an)! 

21. Kenako 
adayang'anayang'ana (Nkhope za 
anthu). 

22. Kenakonso adachita tsinya 
Ndikukwinya nkhope (kwambiri 
Ndi mkwiyo). 

23. Kenakonso adanyoza 
Choonadi ndi kudzikweza 
(Posachivomereza), 









®\te*k&%%ty% 






&K#W$i 















©j£===CM»b^.>ijto 



Surat 74. Al-Muddaththir Juzu 29 1291 T ^ *>i 



vt yjdiSj^- 



24. Adati: "Sichina ichi 
(Qur'an) koma Ndi matsenga 
amene adalandiridwa (Kuchokera 
kwa amatsenga akale), 

25. Sichina ichi koma ndi mawu 
aanthu!" 

26. Posachedwa ndimlowetsa 
ku 'Saqara' 

27. Nanga ndi chiyani 
chakudziwitsa Za 'Saqara'? 

28. (Ndi moto umene) susiya 
(mnofu) Ndiponso susiya (fupa), 

29. Umapsereza ndi kudetsa 
khungu. 

30. Kumeneko kuli khumi ndi 
asanu Ndi anayi (alonda 
oyang'anira Motowo.) 

31. Ndipo sitidaike oyang'anira 
kumoto (Kukhala anthu) koma 
angelo; Ndipo sitidaike 
chiwerengero chawo Koma 
ndimayeso kwa amene 
Sadakhulupirire, ndi kuti 
atsimikize Amene adapatsidwa 
mabuku (zimene Qur'an ikunena 
za chiwerengero cha Angelo 
akumoto) ndiponso kuti 
Chionjezeke chikhulupiriro kwa 
amene Akhulupirira, ndikuti 
asapeneke Amene adapatsidwa 
mabuku pamodzi Ndi okhulupirira. 
Ndiponso kuti amene m'mitima 
Mwawo muli matenda (matenda 






Sfirat 74. AI-Muddaththir Juzu 29 



1292 ™*j*-i 



Vi jJjAtoj^-. 



Achinyengo) komanso 
osakhulupirira Anene: "Kodi 
Mulungu akulinganji pa Fanizo 
limeneli?" Momwemo Mulungu 
Akumulekerera kusokera amene 
Wamfuna, ndipo akumuongola 
amene Wamfuna ndipo palibe 
amene angadziwe Magulu a 
nkhondo a Mbuye wako Kupatula 
lye mwini.(Kutchula moto ndi 
Zam'kati mwake) sichina koma 
Ndichenjezo kwa anthu. 

32. Sichoncho; ndikulumbirira 
mwezi, 

33. Ndi usiku pamene 
ukuchoka, 

34. Ndi m'bandakucha pamene 
Kukuwala. 

35. Ndithu uwo, (moto wa 
Jahannama) ndi Chimodzi mwa 
malodza aakulu, 

36. Ndi chenjezo kwa anthu, 

37. Kwa yemwe wafuna mwa 
inu Kutsogola (pochita zabwino 
Zokamthandiza tsiku louka kwa 
Akufa) kapena kutsalira (ndi 
Zam'dziko). 

38. Mzimu uliwonse ukakhala 
chikole Ndi zimene udachita. 

39. Kupatula akudzanja lamanja 
(Asilamu Amene adadzimasula 
okha Potembenukira kwa Mulungu). 



*-<&& 



®PcJs\ 



Surat 74. AHVIuddaththir Juzu 29 1293 t * *>» 



Vi yjdUj^ 



40. (I wo) adzakhala m'minda 
(yosasimbika Kukongola kwake) 
akufunsana wina ndi Mnzake; 

41. Za anthu oipa, 

42. (Kuti): "Nchiyani 
chakulowetsani Kumoto?" 

43. Adzanena: "Sitidali m'gulu 
la Omwe adali kupemphera 
(Swala) 

44. Ndiponso sitidali 
kuwadyetsa Masikini. 

45. Koma tinkangomira 
(m'zachabe ndi Zabodza) pamodzi 
ndi omira M'menemo 

46. Ndiponso tidali kukana za 
tsiku la Malipiro 

47. Mpaka imfa idatifika." 

48. Siwudzawathandiza 
uwomboli wa Awomboli. 

49. Kodi ali ndi chiyani iwo 
pakuti Azinyozera chenjezoli 
(limene lili Qur'an?) 

50. (Akuyenda mothamanga 
kuti asamve Chenjezoli) ngati kuti 
iwo ndi Mbidzi zothawa, 

51. (Zimene) zathawa mkango. 

52. Ati akufuna aliyense mwa 
iwo Apatsidwe kalata 
zotambasulidwa (Zimene 
zitsimikize uthenga wa Mneneri 
Muhammad{SAW}); 



k^m^o, 






®Q&X\&&£\H 



k.&Ll\L&?4& 



®, 



'•T> > -^> 



*&$\'rj&& 












Surat 74. Al-Muddaththir Juzu 29 1294 t S * j*-» 



v t >di 3jj- 



53. Sichoncho! Koma kuti iwo 
Sakuopa tsiku lomaliza. 

54. Sichoncho! Ndithu, ichi 
(Qur'an) Ndichikumbutso 
(chokwanira); 

55. Amene wafuna 
achikumbukire (Amene sakufuna 
ndizake)! 

56. Ndipo sangakumbukire 
pokhapokha Mulungu atafuna. lye 
ndiye Amene Ali woyenera 
kumuopa, ndiponso Ndiye Mwini 
kukhululukira (Amene akumuopa). 










Surat 75. Al-Qiyamah Juzu 29 



1295 



Y**j*-» 



V© JUUii ojj-- 




Surayi ikufotokoza zakuuka kwa anthu kuchokera kwa akufa 
ndi kuweruzidwa pa zochita zawo. Ndiponso ikufotokoza za 
tsiku la chimaliziro ndi zoopsa zake ndi kumuuza Mtumiki 
(SAW) kuti Qur'an idzasonkhanitsidwa pa chifuwa chake. 

Yadzudzula kwabasi amene akukonda kwambiri moyo 
wadziko ndikusalabadira za moyo wa tsiku lomaliza. Ndipo 
yafotokoza mmene zidzakhalire nkhope za okhulupirira ndi 
nkhope za okanira. Yakambanso za madandaulo amene munthu 
amakhala nawo imfa ikamfikira chifukwa chosakwaniritsa 
zimene Mulungu adamlamula. 

Ndipo surayi yamaliza ndi kutizindikiritsa kuti munthu 
adzauka ku imfa tsiku lomaliza. 




Surat 75. Al-Qiyamah Juzu 29 1296 * * *>» 



Vo 3^Ufl]l 5j_^» 



Surat Al-Qiyamat LXXV 



w 



$^Wr? 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira tsiku 
lachimaliziro. 

2. Ndikulumbiriranso mzimu 
Wodzidzudzula (pa cholakwa 
Chimene wachita. Ndithu, 
Mudzaukitsidwa; mafupa anu 
Omwazikana atasonkhanitsidwa.) 

3. Kodi munthu akuganiza kuti 
Ife (Amene tidamlenga kuchokera 
Popanda chilichonse) sitidzatha 
Kusonkhanitsa mafupa ake 
(ofumbwa)? 

4. Iyayi, Ife tikhoza 
(kutisonkhanitsa) Ndi 
kutilongosola bwino timizere 
Takunsonga kwa zala zake. 
(Mafupa Ake ndiye osanena)! 

5. Koma munthu akukanira 
(kuukaku) Ncholinga chopitiriza 
kuchita zoipa M'masiku omwe 
akudza mtsogolo Mwa moyo wake 
onse. 

6. Akufunsa (mwa chipongwe): 
"Kodi Lidzakhala liti tsiku la 
chimaliziro?" 

7. Pamene maso adzangoti 
tong'oo (Ndi mantha), 



0M3\^3\^J^r 



-2> 












&<X\'J>$^i\%£# 



©*y»j£t$<j£4 



&^\&\i$ 



Surat 75. Al-Qiyamah Juzu 29 1297 t ^ *>» V* i*UJi 5^ 



8. Ndi kuchoka kuwala kwa 
mwezi, 

9. Ndipo dzuwa ndi mwezi 
Ndikusonkhanitsidwa. 

10. Munthu adzanena tsiku 
limenelo: "Nkuti kothawira 
(chilangochi?)" 

11. (Adzauzidwa): "Iyayi, (iwe 
munthu) Palibe pothawira (pako)!" 

12. Tsiku limenelo kobwerera 
(anthu) ndi Kwa Mbuye wako basi. 

13. Tsiku limenelo munthu 
adzauzidwa Zochita zake zimene 
adazitsogoza Ndi zimene 
adazichedwetsa. 

14. Koma munthu adzadzichitira 
umboni Yekha pa mzimu wake, 

15. Ngakhale atapereka 
madandaulo ake (Otani kuti 
apulumuke nawo Sadzapulumuka). 

16. Usaigwedezere (Qur'an) 
lirime lako (Pamene 
ikuvumbulutsidwa) kuti 
Muifulumirire (kuiwerenga ndi 
kuisunga Mumtima). 

17. Ndithu, ndiudindo Wathu 
Kuisonkhanitsa (mumtima mwako) 
Ndi kukhazikitsa kawerengedwe 
Kake (palirime lako). 

18. Pamene tikukuwerengera 
iwe Tsatira kuwerenga kwakeko 
(Uku uli chetee). 






iSZl ' U 9 t S ( *9* 



%W&kZ&&& 



eVtim%$\% 



Surat 75, Al-Qiyamah Juzu 29 1298 * * *>» V © butt a^ 



19. Kenako, ndithu, ndiudindo 
Wathu Kulongosola (zimene 
sukumvetsa), 

20. Iyayi koma mukukonda 
moyo Wapadziko. 

21. Ndipo mukusiya moyo wa 
Tsiku lomaliza. 

22. Nkhope zina tsiku limenelo 
Zizawala kwambiri (ndi Mtendere), 

23. Zili kumuyang'ana Mbuye 
wawo 

24. Ndipo nkhope zina tsiku 
limenelo Zidzakhala zoziya. 

25. Zikuyembekezeka kuti 
zilandira Tsoka lodula msana. 

26. Sichoncho! Pamene mzimu 
udzafika Pa nthitimtima, (pomwe 
pakumana Mafupa am'mapewa). 

27. Ndipo ndikunenedwa ndani 
Angamchiritse 

28. Ndipo (iye mwini wake), 
nkutsimikiza Kuti ndithu uku 
ndikusiyana (ndi dziko Lapansi) 

29. Ndipo miyendo 
idzasanjikizana; (Iyi ndi nthawi 
yochoka mzimu). 

30. Tsiku limenelo koperekedwa 
(anthu Onse) nkwa Mbuye wako; 

31. Ndipo sadakhulupirire 
komanso Sadapemphere swala 
(zisanu), 



«>fc©L£&£ 



!ffl*ai&tftf*^ 









&$&%>& 



©a^i^is^ 



Surat 75. AI-Qiyamah Juzu 29 1299 Y * *>■! Vo &\Jti\ ©j^- 



32. Koma (m'malo mwake) 
adatsutsa ndi Kunyoza. 

33. Kenaka adapita kubanja 
lake (Uku akuyenda) monyada. 

34. Kuonongeka nkwako (iwe 
wotsutsa)! Kuonongeka zedi! 

35. Ndiponso kuonongeka 
Nkwako! kuonongeka zedi! 

36. Kodi munthu akuganiza kuti 
angosiidwa Chabe? 
(Sadzaweruzidwa)? 

37. Kodi sadali dontho la 
umuna Umene udafwamphuka 
(M'chiberekero)? 

38. Kenako adakhala nthinthi 
(Ntchintchi) ya magazi, ndipo 
Adamlenga ndi kumlinganiza 
(monga Munthu), 

39. Ndipo adalenga kuchokera 
mmenemo (M'magazi) omwewo 
mitundu iwiri: Mwamuna ndi 
mkazi. 

40. Kodi (lye amene 
adayambitsa Chilengedwe 
choyambachi) sangathe Kuwapatsa 
moyo akufa? 
















Surat 76. Al-Insan Juzu 29 1300 * * >>' V'l Ouj^i 3j^ 




M'surayi muli mawu olongosola chiyambi cha kalengedwe 
ka munthu ndi kuti zili kwa munthu kuyamika Mulungu kapena 
kumkana. 

Yafotokoza mwachidule mphoto za okana. Ndipo yafotokoza 
motambasula za mtendere wa Mulungu umene akaupereka kwa 
anthu Ake okhulupirira. 

Kenako yamulamula Mneneri (SAW) ndi kumfotokozera 
chisomo chili pa iye pomvumbulutsira Qur'an yolemekezeka. 
Ndipo yamulamula kupirira ndi kupitiriza kumvera. 

Amene akukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi ndi 
kusiya moyo wa tsiku lomaliza yawachenjeza. Ndipo 
yafotokozanso kuti mma aya amenewa muli maphunziro ndi 
kuti palibe amene angapindule ndi maaya amenewa koma 
kupyolera mchifuniro cha Mulungu. 




Siirat 76. Al-Insan Juzu 29 I 1301 I * * *>■* 



VI OUJ^I Sj^- 



SuratALIns&n LXXVI 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambih, Wachisoni 

1. Ndithu, munthu idampita 
nthawi Yaitali kwambiri 
(asanauziridwe Mzimu) pomwe 
sadali chinthu Chotchulidwa. 

2. Ndithu, Ife tamlenga munthu 
kuchokera Kumbewu ya umunthu 
yosanganikirana (Ya mkazi ndi ya 
mwamuna) kuti Timuyese mayeso 
(ndi malamulo Athu); Choncho 
tidampanga kukhala wakumva Ndi 
wopenya; (amve mawu a 
Mulungu) Ndi kuti aone zisonyezo 
Zake). 

3. Ife tidamlongosolera njira 
yoongoka: Kukhala wokhulupirira 
kapena wotsutsa (Zonse zili kwa 
iye). 

4. Ndithu, Ife okana 
tawakonzera unyolo 
(Wam'miyendo yawo) ndi magoli 
(Am'manja ndi m'makosi awo) ndi 
Moto waukali woyaka. 

5. Ndithu, oona pa 
chikhulupiriro chawo Adzamwa 
vinyo, chosanganizira chake 
Chidzakhala (madzi a) kaafura. 

6. (Kaafura ameneyo) 
ndikasupe amene Azikamwapo 



^«W* 



-^ 












Surat 76. Al-Insan Juzu 29 1302~~| * * ^ 



vn ol-j^ioj^ 



akapolo a Mulungu ndi 
Kumtulutsa (paliponse pamene 
afuna) Kumtulutsa mofewa. 

7. (Amene) akukwaniritsa 
zimene adalonjeza (Okha kwa 
Mulungu), ndiponso Akuopa tsiku 
(lalikulu) limene Zoipa zake 
zidzakhala zofalikira Ponseponse. 

8. Ndipo amadyetsa chakudya 
masikini, Amasiye ndi ogwidwa pa 
nkhondo, Pomwe iwo 
akuchifunanso. 

9. Amanena (chamumtima 
akamapereka Chakudyacho): 
"Tikukudyetsani Chifukwa 
chofuna chikondi cha Mulungu 
basi; sitikufuna kwa inu Malipiro 
kapena kuthokoza. 

10. Ndithu, ife tikuopa kwa 
Mbuye wathu Tsiku lokhwinyata 
nkhope ndi mavuto Aakulu." 

11. Ndipo Mulungu 
adzawateteza Kumavuto a tsiku 
limenelo ndiponso Adzawapatsa 
Mtendere ndi chisangalalo. 

12. Ndipo adzawalipira 
chifukwa cha kupirira Kwawo 
munda wa mtendere ndi Nsalu 
zaveleveti; 

13. Atatsamira m'menemo 
pamabedi (Amtengo wapatali); 
sazamva M'menemo kutentha kwa 
dzuwa Kapena kuzizira. 



+* \c 






e$J£&JP&%>&&&%\ 



bl l#» '"CAS"' l* >f' t" fj i " 






Surat 76. Al-Insan Juzu 29 I 1303 I t <\ *j*-i 



VI OUJ^t 5 J>( - 



14. Mithunzi yake 
ikawayandikira iwo Ndipo mikoko 
yazipatso idzatewa Pafupi (moti 
munthu atha kuthyola Ali 
chigonere). 

15. Ndipo adzakhala 
akuzunguliridwa (Ndi otumikira) 
uku atatenga zomwera Zasiliva ndi 
matambula onyezimira Ndiponso 
olangala. 

16. Zolangala zopangidwa ku 
siliva, atalinga Bwino zakumwazo 
(malinga ndi kufuna Kwawo). 

17. Ndipo (anthu abwino) 
akamwetsedwa Kumeneko vinyo, 
chosakanizira chake Chikafanana 
ndi zanjabila (chikasu). 

18. M'menemo muli kasupe 
wotchedwa Salisabila, 

19. Ndipo azikawazungulira 
anyamata Osasinthika 
(chilengedwe chawo,) Utawaona 
(chifiikwa cha kukongola Kwawo 
ndi kuwala kwa nkhope zawo) 
Ungawaganizire kuti ndi ngale 
Zomwazidwa. 

20. Ndipo ukadzaona kumeneko 
(ku Jannah) ukaona mtendere ndi 
ufumu Waukulu. 

21. Pamwamba pawo 
padzakhala nsalu Zaveleveti 
zopyapyala, zobiriwira Ndi nsalu 
zaveleveti zochindikala, 






))\,9 ,'£ 9'\'y 



dj/j£&> 



\* 9 '/A' 9 *'*--* *• 9 T \"\'i 



m^^\y^^^^ 









J^j^k^j}^ &jffi\$*5 



®]%&V\j& 



Surat 76. Al-Insan Juzu 29 



1304 Tl*>i 



V\ OUJ^I 5jj^ 



Akavekedwa m'manja mwawo 
zibangiri Zasiliva; Mbuye wawo 
akawamwetsa Chakumwa china 
choyera kwambiri. 

22. (Akawauza kuti:) "Ndithu 
iyi ndi mphoto Yanu ndipo ntchito 
Zanu ndi zolandiridwa." 

23. Ndithu, Ife taivumbulutsa 
kwa iwe Qur'an 
mwapang'onopang'ono (kuti 
Uisunge bwino, usaiwale) 

24. Choncho, pirira ndi lamulo 
la Mbuye Wako ndipo usamvere 
wamachimo Kapena wokanira 
Aliyense mwa iwo. 

25. Ndipo kumbukira dzina la 
Mbuye Wako; mmawa, ndi 
madzulo (swala za Subuhi, Zuhri 
ndi Asri). 

26. Ndipo usiku mlambire lye, 
(swala YaMagharib ndi Isha); 
ndiponso Umulemekeze usiku 
nthawi yaitali (Popemphera sunna 
za tahajudi) 

27. Ndithu awa akukonda 
umoyo Wadziko lapansi, ndipo 
akulisiya Kumbuyo tsiku lovuta. 

28. Ife ndi amene tidawalenga 
ndipo Tidalimbika kalengedwe 
kawo; ndipo Titafuna 
tingabweretse ena onga iwo 
(Omvera Mulungu) kulowa 
m'malo Mwawo. 



%&Gtrfe%&\&& 



k\**r?4 



®%&uX$\®&&&<>%\ 






8Wtt#4p>a#6 






i<\ 'r. 9 * '"ft' 9 "i <.' ?> S ZX' 9 >'\ 



Surat 76. Al-Insan Juzu 29 



1305 



M >>» 



VI OUJ^I 6jj~> 



29. Ndithu ichi ndichikumbutso 
Choncho amene Afuna atsata njira 
yopitira kwa Mbuye wake 
(pomukhulupirira ndi 
Kumumvera). 

30. Koma simungafune nokha 
chilichonse Pokhapokha atafuna 
Mulungu, ndithu Mulungu ndi 
Wodziwa, Wanzeru. 

31. Akumlowetsa amene 
wamfuna Kuchifundo Chake; 
koma oyipa Wawalinganizira 
chilango chowawa Kwambiri. 













Surat 77. Al-Mursalat Juzu 29 I 1306 I t * *>H VV o*-jI» 5j>- 




Mfundo yofiinika imene surayi ikufotokoza ndi kuuka ku 
imfa pa tsiku la Kiyama. Ndipo ikupereka kwa anthu zizindikiro 
zosonyeza kuti zimenezo zidzachitika pakuti Mulungu adachita 
zazikulu kuposa zimenezo. 

Mawu akuti: "Kuwonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli 
pa otsutsa"abwerezedwabwerezedwa kokwanira khumi pofuna 
kuwaopseza ndi kuwachenjeza amene akukana zakuuka 
kuchokera ku imfa, ndi kuti adzakumana nacho chilango 
chachikulu patsikulo. 

Kenako ikuuza anthu olungama nkhani yabwino ponena kuti 
mtendere ndi chisangalalalo cha Mulungu zidzakhala pa iwo. 

Ndipo surayi yamaliza ndi kunenetsa kuti kuonongeka kuli pa 
okana Mulungu amenenso sakhulupirira Qur'an. 




Surat 77. Al-Mursalat Juzu 29 1307 Y * tjA-i VV o^UjLi 5^ 



S«ra* Al-Mursalat LXXVII 



M 



mm& 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira mphepo 
yomwe Ikuomba motsatizana. 

2. Ndi mphepo yamkuntho. 

3. Ndi mphepo yobalalitsa 
mitambo ndi Mvula. 

4. Ndi ma aya osiyanitsa Pakati 
pachoona ndi chonama; 

5. Ndi angelo opereka 
chivumbulutso Kwa aneneri. 

6. Kuti chichotse madandaulo 
ndiponso Kuti chikhale chenjezo; 

7. Ndithu, zimene 
mukulonjezedwa (kuti Chimaliziro 
chidzakhalapo) Zidzachitikadi 
(popanda chipeneko), 

8. Pamene nyenyezi 
zidzafafanizidwa (Kuwala kwake 
ndi kuchotsedwa M'malo mwake). 

9. Ndiponso pamene thambo 
Lidzang'ambidwa. 

10. Ndi pamenenso mapiri 
adzachotsedwa M'malo mwake 
ndi kuperedwa (Kukhala fumbi). 

11. Ndi pamene aneneri 
adzasonkhanitsidwa Pa nthawi 



Q^lfc^J)!^ 



-Ci 






©tti^cJ^J^l'S 



<teaa» 



Surat 77. AI-Mursalat Juzu 29 I 1308 I T * *>i VV o*-^ 5jj- 



yake, (kuti apereke umboni 
Kumibadwo yawo). 

12. Kodi nditsiku lanji 
adzichedwetsera (zinthu 
Zikuluzikulu kuti zizachitike). 

13. Nditsiku la chiweruziro 
(pakati Pa zolengedwa). 

14. Nchiyani chakudziwitsa za 
tsiku la Chiweruzirolo.? 

15. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku limenelo Kuli pa otsutsa 
(lonjezo Lathu la Kuuka ku imfa) 

16. Kodi sitidawaononge 
(anthu) akale (Chifukwa cha 
machimo awo, monga Anthu a 
Nuhu, Adi ndi Samudu)? 

17. Kenako titsatiza ena (okana 
Mulungu m'kuonongekako monga 
Tidawachitira oyamba), 

18. Chomwecho tiwachitiranso 
Ochimwa. 

19. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa 
(Lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). 

20. Kodi sitidakulengeni 
kuchokera Kumadzi onyozeka, 
(madzi ambewu ya Munthu)? 

21. Kenako tidawaika pamalo 
Okhazikika (kuti chilengedwe 
chake Chikwanire pamenepo), 

22. Mpaka nyengo yodziwika 
(imene Tidaipima kuti mwana 
abadwe). 






' 9 -lift J A* l>* s*u 









Siirat 77. Al-Mursalat Juzu 29 1309 Y a ^j*-i VV 0*^1 5^ 



23. Tidaipima nyengoyo; 
taonani Kupima bwino Ife opima! 

24. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa 
(Lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). 

25. Kodi sitidaichite nthaka 
kukhala Yofungatira, 

26. Amoyo ndi akufa? 

27. Ndipo tidaika m'menemo 
mapiri Ataliatali (olimbitsa 
nthaka), Ndipo takumwetsani 
madzi okoma. 

28. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa 
(Mtendere umenewu). 

29. (Kudzanenedwa kwa okana 
tsiku la Chimaliziro:) Pitani 
kuzimene Mudali kuzitsutsa zija. 

30. Pitani kumthunzi (wautsi wa 
Kumoto) wa nthambi zitatu, 

31. Simthunzi (wamtendere) 
ndiponso Siwotchinjiriza 
kumalawi a moto." 

32. Ndithu uwo (moto 
umenewu) umaponya Mphalikira 
(mbaliwali) zazikulu ngati Nyumba, 

33. Zonga ngati ngamira 
zachikasu. 

34. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku limenelo Kuli pa otsutsa 
(zimenezi). 






s* • f^Tt \ ' 9 t$\ 9 ' 









Surat 77. Al-Mursalat Juzu 29 1310 Y H *>i VV o^>i Sj^ 



35. Hi ndi tsiku lomwe 
Sadzalankhula. 

36. Ndipo sadzapatsidwa 
chilolezo (Choyankhulira) kuti 
apereke madandaulo Awo. 

37. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa (za 
Tsiku limenelo). 

38. (Adzauzidwa kuti): Hi ndi 
tsiku loweruza (Pakati pa abwino 
ndi oipa Takusonkhanitsani inu 
(otsutsa Muhammad {SAW}), ndi 
akale (otsutsa aneneri akale). 

39. Ngati muli ndi ndale 
(yodzipulumutsira Kuchilango 
Changa) ndichiteni ndaleyo! 

40. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku limenelo kuli Pa otsutsa 
(lonjezo la Mulungu). 

41. Ndithu, oopa (Mulungu 
tsiku limenelo) Adzakhala 
mumthunzi ndi M'mitsinje, 

42. Ndipo adzakhala ndi zipatso 
zomwe Azidzazifuna. 

43. (Kudzanenedwa kwa iwo): 
"Idyani, Imwani mokondwa 
chifukwa cha Zabwino zomwe 
mudali kuchita (Muumoyo wa 
dziko lapansi). 

44. Ndithu umo ndi mmene Ife 
timawalipirira Ochita zabwino. 









©Q^^irA^ 



^^^&^^yf^ 



^^%a^(S 






^JcM&^Ot 






&~&^^™ A 



Surat 77. Al-Mursalat Juzu 29 1 1311 | Y ^ tji-i VV o^L-^li Sj^- 



45. Kuonongeka kwakukulu 
Tsiku limenelo kuli pa Otsutsa 
(mtendere wa Mulungu) 

46. Idyani, sangalalani 
pang'ono M'kanthawi kochepa; 
ndithu, Inu ndinu ochimwa 
(chifukwa Chakumphatikiza 
Mulungu ndi Zolengedwa). 

47. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa 
(Mtendere wa Mulungu). 

48. Ndipo kukanenedwa kwa 
iwo: "Weramani, (pembedzani 
Mulungu)" Sakuwerama. 

49. Kuonongeka kwakukulu 
tsiku Limenelo kuli pa otsutsa 
(Malamulo a Mulungu). 

50. Kodi ndi nkhani iti imene 
Adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi 
(Qur'an)? 



tftff *9&L9\9' 



%^m^-& 













Surat 78. An-Naba> Juzu 30 



1312 



*>« 



VA 



5 J>" 



^^ 



r Lr\Jr=2;^>^~»^ ^^ r 



SURAT AN-NABA' LXXVIII 




Surayi yanenetsa zakuuka m'manda, ndipo yaopseza amene 
akukaikira zimenezi. Ndiponso yasonyeza kutheka kwa 
zimenezo posonyeza zinthu zomwe zikuonetsa mphamvu za 
Mulungu. Ndipo yatsimikiza za kuukako potchula zina mwa 
zisonyezo zake. Kenako yatchula mabwerero a anthu oipa, 
opyola malire. Ndi mabwerero a anthu abwino, oopa Mulungu. 
Ndipo yamalizira ndikuchenjeza za tsiku loopsalo. 



Surat An-Naba ' LXXVIII 



m 



0^\^\&\*r 



-& 






®v&Z& 



A 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kodi akufunsana zachiyani? 

2. Za nkhani yayikulu ija. 

3. Imene iwo akusiyana 
(maganizo). 1 

4. Aleke (zimenezo) adzadziwa 
posachedwapa. 2 

5. Ayi, ndithu, aleke 
(zimenezo); Posachedwapa 
adzadziwa zoona Zake (pamene 
chilango chidzawatsikira) 3 

1 Nkhani yaikulu imene akafiri (anthu osakhulupirira Mulungu) adali kufunsana 
wina ndi mnzake ndi nkhani yakuuka tsiku la Kiyama t ndi uneneri wa Mtumiki 
Muhammad. Amafunsana kuti, "Kodi nzoona tidzadzuka m'manda, nanga 
nzoona kuti Muhammad ndi Mneneri?" Adali kufunsananso kuti, "Kodi zakuti 
Mulungu ndi Mmodzi ndi zoona?" 

2 Kulankhula koti: "Kallaa" kwanenedwa kwambiri m'Qur'an. Tanthauzo lake 
nthawi zina ndikuletsa, nthawi zina ndikutsimikiza. Choncho mawuwa 
amatanthauzidwa malinga ndi momwe chiganizocho chilili. 

3 Mulungu, apa, akuwauza kuti asiye kuganizira zinthu zopanda pake. Kodi 
sadadziwebe mpaka tsopano kuti Muhammad ndi Mneneri wa Mulungu, 



®&&&&P 



Surat 78. An-Naba' Juzu 30 1313 r • *> 



VA l_Jl 3^ 



6. Kodi sitidachite nthaka 
kukhalaNgati choyala? 1 

7. Ndi mapiri ngati zichiri 
(zolimbitsa Nthaka)? 

8. Ndipo takulengani mitundu 
iwiri (Amuna ndi akazi). 

9. Ndipo tidachita tulo tanu 
kukhala Mpumulo (kumavuto a 
ntchito). 

10. Ndipo taupanga usiku 
kukhala ngati Chovala 
(pokuvindikirani Ndi mdima 
wake). 

11. Ndipo tapanga masana 
kukhala Nthawi yopezera zofunika 
pa moyo; 

12. Ndipo tamanga pamwamba 
panu thambo Zisanu ndi ziwiri 
zolimba; 

13. Ndipo tidapanga nyali 
yowala ndi Yotentha kwambiri 
(dzuwa); 

14. Ndipo tawatsitsa madzi 
otsika Mwamphamvu kuchokera 






*«lft&3SE3 



£ 1183*0% 



to®zaqm% 



••<, 



m<>j$&$& i s& 



©V>t£ j>l£ i^H^Xi>5 



^sW6^^a»^$ts 



ndikuti Mulungu ndi Mmodzi yekha? Ndikutinso kuli tsiku lomaliza; pamene 
munthu aliyense adzalipidwa pazimene adachita? Basi tsiku lomaliza 
likadzawafikira adzadziwa kuti zimene adali kuwauza Mneneri nzoona. 
1 Kuyambira aya iyi, kudzafika aya 16, Mulungu akusonyeza anthu Ake 
madalitso ambiri omwe wawadalitsa nawo kuti azindikire kuti Mwini kupereka 
madalitso amenewa m'dziko sangawasiye anthu Ake m'kusokera popanda 
kuwatumizira munthu wowaongolera kunjira yabwino, ndikuwadziwitsa 
zamtendere wapadziko ndi tsiku lomaliza. Ndikuti Mulungu amene adapanga 
zonsezi palibe chimene angachilephere. Ndipo tanthauzo la choyala, apa, ndi 
pamalo poti nkutheka munthu kuchita chimene akufuna pa moyo wake. 
Tanthauzo lake sikuti dothi lakhala ngati mkeka wa pabedi ayi. 



Surat 78. An-Naba' Juzu 30 



1314 



'J* 



VA 



0j^ 



ku mitambo, Ya mvula; 

15. Kuti titulutse ndi madziwo 
mbewu Ndi m'mera, (chomwe ndi 
chakudya Cha anthu ndi nyama). 

16. Ndi minda yothothana 
nthambi za Mitengo. 

17. Ndithu, tsiku la chiweruzo 
ndi Nthawi imene 
idakhazikitsidwa kale, 

18. Tsiku limene lipenga 
(lakuuka) Lidzaimbidwa ndipo inu 
mudzabwera (Kubwalo 
losonkhanirana) muli 
Magulumagulu. 

19. Ndipo thambo 
lidzatsegulidwa (Mbali zonse): 
lidzakhala Makomomakomo. 

20. Ndipo mapiri 
adzachotsedwa m'malo Mwake, 
adzakhala ngati zideruderu. 1 

21. Ndithu, moto wa Jahena 
ukuwadikirira (Oipa). 

22. Mbuto ya opyola malire. 



m&ur& 






©\SUJf< 



$ t* i'*\ " 9 -K'< 9t 



Z<Z > '9 4 



SW^^d*^ 






1 Apa, ndikuti zimene munthu amaziona patsogolo pake nkumaziganizira ngati 
madzi pomwe sali madzi. Choncho pa tsiku limenelo mapiri adzaoneka ngati 
akhazikika monga m'mene adalili pomwe sichoncho, adzakhala ngati thonje 
louluka ndi mphepo. 

2 Jahannamu ndi dzina lamoto wodziwika wa tsiku lomaliza. Apa Mulungu 
akutidziwitsa kuti Jahannamu ndi malo amene akudikira akafiri kuti 
m'menemo akalipidwe malipiro awo chifukwa chokanira aneneri pambuyo 
powasonyeza ztzindikiro zoti iwo ndi aneneri a Mulungu. Ndiponso 
kumulakwira Mulungu pochita zimene adaletsa monga; kukana umodzi wa 
Mulungu, kukana utumiki wa Mahammad (SAW) ndi kukana uthenga wa 
Qur'an. Komanso kugwa mmachimo osiyanasiyana. 



Surat 78. An-Naba' Juzu 30 1315 T * *>i 



VA i — -all 9jy* 



23. Adzakhala m'menemo 
muyaya. 

24. Sadzalawa m'menemo 
kuzizira (Kowachotsera kutentha), 
kapena Chakumwa (chowachotsera 
ludzu lawo); 

25. Kupatula madzi otentha 
Kwambiri ndi mafinya (otuluka 
Mmatupi a anthu a kumoto); 

26. Kukhala malipiro olingana 
Ndi ntchito zawo. 

27. Ndithu iwo sadali 
kuyembekezera Chiwerengero (cha 
Mulungu); 

28. Adatsutsa zizindikiro Zathu 
(Zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi 
Mtsutso waukulu. 

29. Ndipo chinthu chilichonse 
Tachisunga mochilemba. 

30. Basi, lawani (lero chilango 
Changa); Sitikuonjezerani chinthu 
China koma chilango pamwamba 
pa Chilango. 

31. Ndithu, anthu oopa 
Mulungu adzakhala Ndi malo 
wopambana. 

32. Minda ndi zipatso za mphesa. 

33. Ndi mabuthu (anamwali) 
Ofanana misinkhu. 

34. Ndi zipanda zodzaza Ndi 
zakumwa. 















Sfirat 78. An-Naba' Juzu 30 



1316 



r* *>i 



VA I— dl oj^ 



35. Sakamva m'menemo mawu 
opanda Pake kapena bodza. 

36. Amenewa ndi malipiro 
Ochokera kwa Mbuye wako 
Zopereka zokwanira. 1 

37. Mbuye wa kumwamba ndi 
pansi Ndi zimene zili pakati pake; 
Wa Chifundo Chambiri. Palibe 
amene adzakhala ndi Mphamvu 
yolankhulana naye (Pa tsiku 
limenero); 

38. Tsiku limene adzaima Jibril 
Ndi angelo pa mzere (ali 
Odzichepetsa); sadzalankhula 
Aliyense mwa iwo kupatula 
Yekhayo amene adzaloledwa ndi 
Wachifundo Chambiri 
(kulankhula) Ndipo adzanena 
zolondola. 

39. Limenelo ndi tsiku loona, 
(Lopanda chikaiko); choncho 
Amene akufuna adzipezere Malo 
(njira yonkera) Kwa Mbuye wake. 
(Pomugonjera lye pa umoyo uno 
wadziko lapansi). 

40. Ndithu, tikukuchenjezani 
Zachilango chomwe chili pafupi 



i'*<^'\1t'*i '^'''v 



hZm$&^££Z3 



h%\^$&Q0&i 



l> 









®0^»J\|j 



JtfiS&^^jJl^ 






'j&tew$s®&i 



Chipembedzo cha Chisilamu chikuphunzitsa kuti pali zisangalalo ziwiri: 
Chisangalalo cha mzimu ndi chisangalalo cha thupi. Tsono chisangalalo cha 
mzimu ndiko kuyanjana kochokera kwa Mulungu kumene anthu Ake abwino 
adzakupeza. Chisangalalo cha thupi ndi monga m'mene afotokozera mu ayah 
iyi ndi msura zina: Zokondweretsa monga minda, akazi okongola, mowa 
(osaledzeretsa) ndiponso sikudzakhala kumva chilichonse chokhumudwitsa. 
Taonani, zoledzeretsa ndi zoletsedwa padziko lino lapansi chifukwa cha zoipa 
zake. Koma zoledzeretsa za patsiku la Kiyama zidzakhala zopanda zoipa. 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 1317 T * *>-» V* oIpjUi Sj^ 



Kudza; tsiku limene munthu 
Adzayang'ana zimene adatsogoza 
Manja ake, ndipo kafiri 
(wosakhulupirira) Adzanena: 
Kalanga ine! Ndikadakhala Dothi, 
(kuti ndisalangidwe chilango 
Chikundiy embekezachi) . 








SURAT AN-NAZPAT LXXIX 



Surayi yayamba ndikulumbira potsimikizira kuti kuli kuuka. 
Ndipo yatsatiza nkhani ya Musa ndi Firiauna ndicholinga 
chomtonthoza Mtumiki (SAW) kumavuto omwe ankakumana 
nawo panjira yolalikira. Yatsatizanso kulongosola za zimene 
zikuwayembekezera opyola malire ndi achinyengo pa tsiku 
lomaliza. Ndipo yamalizira ndi funso la amushirikina lofunsa 
zanthawi ya tsiku lomaliza ndikulongosola kuti ntchito ya 
Mtumiki (SAW) ndi kuchenjeza omwe akuopa za tsikulo. 
Koma iye sadziwapo kanthu za nthawi yakudza Qiyama. 



Surat An-Nazi'at LXXIX 



llff^^ 



'JL 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira (angelo) 
Amene amazula (mizimu ya 
Osakhulupirira) mwamphamvu. 1 



Q 



)^l^l^ 



^■^ 



&§j*<%Pj$j 



(Ndime 1-5) M'Qur'an nthawi zambiri Mulungu amalumbirira zolengedwa 
Zake; zamoyo ndi zopanda moyo, zooneka ndi zosaoneka. Cholinga 
ndikutilimbikitsa kuti tikhale olingalira luso Lake pa chinthu chilichonse 
chimene wachilumbirira kuti tizindikire ulemerero Wake ndi mphamvu Zake 
zoposa. 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 



1318 



V. *jJfc-» VH OlPjlJlSjj^ 



2. Ndikulumbiriranso (angelo) 
Amene amachotsa (mizimu ya 
Okhulupirira) moleza. 

3. Ndi omwe amasambira (nayo 
Mizimuyo) mumlengalenga (ponka 
nayo ku malo ake Oyembekezera). 

4. Ndi iwo amene akupikisana 
Pokwaniritsa malamulo a 
Mulungu. 

5. Ndi iwo (angelo) amene 
Akulongosola malamulo (Ake). 
(Ndithudi inu anthu mudzauka 
Kwa akufa). 

6. Patsiku lomwe (lipenga 
loyamba Lidzaimbidwa), dziko 
lapansi ndi Mapiri ake 
zidzagwedezeka (ndipo Aliyense 
adzafa). 

7. Ndipo kudzatsatira kuyimba 
kwa Lipenga lachiwiri (kumene 
Kudzaukitsa akufa onse). 

8. Tsiku limenelo mitima 
idzanjenjemera Ndi kuopa, 

9. Maso a eni mitimayo 
adzakhala Ozyolika (chifukwa 
chamadandaulo); 

10. (Osakhulupirira) akunena: 
"Kodi nzoona tidzabwezedwa 
Pambuyo pa imfa monga tidalili 
kale?" 

11. "Pomwe ife titakhala 
mafupa Ofumbwa (tingabwezedwe 



?' u in.' 



^*a ' Hill '• 9 >£ '>' 



t&$\\2& 






©Aj^^U;W>\ 



mV\&£%3$> 



&%j$U&M\'& 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 



1319 



*j* 



V^ OlPjldl dj>- 



ndi Kuukitsidwa mwa tsopano)?" 

12. Adanena (mokanira ndi 
mwachipongwe): "Choncho 
kubwerera kumeneko ngati 
Kudzakhalepodi kudzakhala 
kotaika (Ndi kopanda phindu kwa 
ife. Pomwe Ife sindife oyenera 
kutaika)" 

13. (Musaganize kubwererako 
nchinthu Chovuta). Ndithundithu 
Kiyamayo ndi Nkuwo umodzi. 

14. Mwadzidzidzi (zolengedwa 
zonse) Zidzangoona zili padziko 
Latsopano (zili zamoyo). 

15. Kodi yakufika (iwe 
Mtumiki) (SAW) Nkhani ya 
Musa? 1 

16. Pamene Mbuye wake 
adamuitana pa Chigwa choyera 
(chotchedwa) Tuwaa, 

17. (Adamuuza kuti) pita kwa 
Farawo Ndithu, iye wapyola 
malire, (Mkudzitukumula kwake 
ndikupondereza Anthu). 

18. Umuuze kuti "Kodi ukufuna 
Kudziyeretsa?" 

19. "Ndikuti ndikuongolere kwa 
Mbuye wako kuti uzimuopa?" 



©*r^ 



&S3\V$$i 









1 Kuyambira aya iyi mpaka aya 26 Ambuye Mulungu akumtonthoza mneneri 
Wake pomuuza nkhani ya Mneneri Musa momwe Farawo adamkanira, ndikuti 
asaganize kuti vutoli lampeza iye yekha koma kuti aneneri enanso akale 
lidawaonekeranso. Ndiponso m'ma ayah amenewa muli chenjezo kwa akafiri 
kuti aope Mulungu kuti asawalange monga adamulangira Farawo ndi anthu 
ake amene adali kutsutsana ndi Mulungu. 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 1320 T • *>i V* oipjUi 5jj~- 



20. (Basi Musa) adamuonetsa 
(Firiauna) chozizwitsa Chachikulu. 

21. Koma (Firiauna) adatsutsa 
(Musa Pazimene adadza nazo zija) 
Ndi kunyoza. 

22. Kenaka adabwerera uku 
akulimbika Kutsutsana naye 
(Mulungu), 

23. Adawasonkhanitsa (afiti) 
uku Akuitana anthu; 

24. Nanena: "Ine ndine mbuye 
wanu Wapamwambamwamba!" 

25. Pamenepo Mulungu 
adamulanga Chifukwa cha mawu 
ake omaliza Ndi oyamba. 

26. Ndithu, pa zimenezi pali 
Phunziro (lalikulu) kwa yemwe 
Akuopa Mulungu. 

27. Kodi kulengedwa kwanu, 
(inu Osakhulupirira kuti muuke) 
Nkovuta kapena thambo limene 
Adalimanga (posonkhanitsa Mbali 
zake zosiyanasiyana Ndikukhala 
chinthu chimodzi)? 1 

28. Adatukula msinkhu wake 
Ndikulikonza bwino (popanda 
Pena pong'ambika kapena 
Posiyana ndi pena). 

29. Ndipo amavindikira mdima 
mu usiku Wake ndipo amatulutsa 






©Lfr>j^3 1$\£m» 7&J 



Q&ffi'&id&b 



1 Tanthauzo lake ndikuti "Kodi chilengedwe chanu nchovuta kwambiri kuposa 
chilengedwe cha thambo pamene inu mukuganiza kuti Mulungu sangathe 
kukudzutsani pambuyo pa imfa?" 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 132 1 T • *>» V^ oIpjlJi 5jj~- 



kuwala Mu usana wake. 

30. Ndipo pambuyo 
pazimenezo, Nthaka adaiyala (kuti 
ikhale Yoyenera kuikhala). 

31. Adatulutsa m'menemo 
madzi Ake (potulutsa akasupe) 
Ndikumeretsa msipu wake (kuti 
Anthu ndi nyama azidya 
msipuwo); 

32. Ndipo mapiri 
adawakhazikitsa 
(Ndikuwalimbika); 

33. (Adachita zonse izi) 
chifukwa Chokusangalatsani inu 
ndiZiwetozanu. 1 

34. Choncho likadzafika tsoka 
lalikulu (Tsiku la Kiyama). 

35. Tsiku limenelo munthu 
adzakumbukira Zimene adachita, 
(zabwino ndi zoipa). 

36. Ndipo moto waukali 
udzawonetsedwa Kwa yense 
openya. 

37. Tsono amene adapyola 
malire (Mmachimo ake), 

38. Ndikudzisankhira (yekha) 
Umoyo wapadziko lapansi, 

39. Ndithu, Jahena ndiwo malo 
ake (Palibe kwina). 



©^po^JS 6J0 $3% 



& 












1 Mu aya iyi Mulungu akusonyeza kuti lye ndi Mwini mphamvu zonse zochitira 
chinthu chilichonse chachikulu kuposa kuwaukitsa akufa; ndiponso akukumbutsa 
ufulu Wake waukulu womwe adatichitira potipatsa zinthu zonsezo kuti 
tithandizike nazo. 



Surat 79. An-Nazi'at Juzu 30 



1322 ?• *jk* V* ou-jUi Sj^- 



40. Tsono amene akuopa kuti 
adzaimirira Pamaso pa Mbuye 
wake, nauletsa Mtima wake ku 
zilakolako zoipa, 

41. Ndithu, munda wa mtendere 
ndiwo Adzakhale malo ake; 
(palibenso Kwina). 

42. Akukufunsa (iwe Mtumiki) 
(SAW) Zanthawi (ya tsiku 
lomaliza kuti) "Idzakhala liti?" 

43. Uli ndi mphamvu yanji iwe 
Yofotokozera tsiku la Kiyamalo? 
(Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo 
Kotero kuti ungaitchule kwa iwo). 

44. Mbuye wako ndi amene ali 
Ndikuzindikira kudza kwake. 

45. Iwe (ntchito yako) 
ndikuwachenjeza Amene akuiopa; 
(osati kulengeza Zanthawi yake). 

46. Tsiku limene adzaiona 
adzakhala Ngati sadakhale 
(padziko nthawi Yayitali), koma 
ngati madzulo Amodzi kapena 
masana ake (nthawi Ya m'mawa). 1 



J28M d*$ iy$& 6&<^SIJ 






1 Apa tanthauzo lake ndikuti adzaona masiku onse amene adakhala m'dziko 
ngati lidali ola limodzi. 



Surat 80. 'Abasa 



Juzu 30 



1323 



*>■' 



A * ^r-P oj>-» 




SURAT 'ABASA LXXX 




Surayi yayamba ndi kudzudzula Mneneri (SAW) pamene 
adasonyeza kusamlabadira Ibn ummu Makutumi, pamene 
adamdzera kudzafuna chiongoko ndi maphunziro. Pamenepo 
nkuti Mneneri (SAW) atatanganidwa ndikulalikira akuluakulu 
achiQuraish uku akuyembekezera kuti mwina angavomereze 
ulaliki wake, ndikuti ngati iwo atero ndiye kuti anthu ambiri 
omwe amatsatira adzavomerezanso. Kenako Surayi yakumbutsa 
munthu zamtendere wa Mulungu umene uli paiye, kuyambira 
pakubadwa kwake mpaka mapeto a moyo wake padziko lino. 
Ndipo yamalizira kunena za tsiku la Kiyama polongosola kuti 
patsikulo anthu adzakhala m'magulu awiri: Gulu la chimwemwe 
la okhulupirira, ndi gulu loipa la okanira. (osakhulupirira). 



Surat 'Abasa LXXX 










M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Adachita tsinya (Mneneri) 
ndi Kuyang'ana kumbali. 1 

2. Chifukwa chakuti adamdzera 
Wakhungu (kudzamfunsa 



Ojfe&\<&$\&\j 



I "ClIJ 






Tsiku lina Mneneri (SAW) atakhala ndi akuluakulu a Aquraishi. Adali 
kuwalalikira za chipembedzo mwachidwi, ndipo adali kuyembekezera kuti 
akavomereza Chisilamu iwo, ndiye kuti anthu owatsatira naonso avomereza. 
Chifukwa anthu ambiri sadalowe Chisilamu poopa atsogoleri awo. Pa nthawi 
imeneyi adatulukira wakhungu wina yemwe ankatchedwa Ibn Ummu Maktum. 
Sadadziwe kuti Mneneri (SAW) ali wotanganidwa Adamukuwira u Ee! Iwe 
Mneneri wa Mulungu! Ndiphunzitse inenso zimene wakuphunzitsa Mulungu." 
Ndipo ankangomubwerezera bwerezera mawu amenewa. Mneneri (SAW) 
pakuti adali ndi chidwi ndi kulalikira akuluakulu aja, Adamchitira tsinya 
wakhungu uja chifukwa chomuonongera ntchito yake; Sadamumvere. Basi 
pamenepa Mulungu akumdzudzula Mneneri Wake pa zomwe adachita posiya 
kumumvera amene adamubwerera kudzafuna chiongoko. 



Surat 80. 'Abasa Juzu 30 



1324 



*>' 



A • j^-p 5jj-» 



Zokhudzana ndi chipembedzo 
Chake pamene iye adali 
Kuyankhula ndi atsogoleri 
AchiQuraishi). 

3. Nanga chingakudziwitse 
nchiyani kuti Mwina iye 
angadziyeretse? (Pomvera ulaliki 
wako Watsopano). 

4. Kapena akumbukira, ndipo 
Kukumbukirako kumthandiza? 

5. Koma amene 
wadzikwaniritsa (ndi Chuma chake 
ndi mphamvu zake), 

6. Ameneyo ndi yemwe 
ukumchitira Chidwi. 

7. Palibe chilichonse pa iwe 
Ngati sadziyeretsa. 

8. Koma amene wakudzera uku 
Akuthamanga (kufuna Maphunziro 
ndi chiongoko), 

9. Ndipo iye akuopa (Mulungu 
Mumtima mwake). 

10. Za iye, iwe sukusamala, 
(Ukuyikira chidwi kwa wina). 

11. Sichoncho! Ndithudi iyi 
(Qur'an) ndi chikumbutso 
(Chenjezo). 1 



afcW^MK 



& Si&\\l"3gL&t'1 



©, 



W&&$$£\ 



0(jwiw|^ul 






®&»£ 2 A^(^> \3il^ 



V It"?' 






(Ndime 11-16) Apa Mulungu akumuletsa Mtumiki Wake kuti asachitenso 
zonga adachitazo ndi kumuuza kuti Qur'an ndi ulaliki chabe, amene afuna 
kulingalira za ulalikiwo, umuthandiza, ndipo amene safuna, kutaika ndi kwake. 
Ndiponso adamufotokozera kuti Qur'an idachokera m'mabuku olemekezeka; 
idachokera ku "Lauhil-Mahfudh" Mabuku omwe ali m'manja mwa Angelo 
olemba, olemekezeka, ochita zabwino omwe ndi abwino kuposa Aquraishi. 



Surat 80. < Abasa Juzu 30 1325 T * >>» 



A* ir -fi 5j>* 



12. Basi, amene wafuna 
alangizika (Ndi Qur'an, ndipo 
amene sakufuna Msiye). 

13. (Malangizowa akuchokera) 
Mmakalata olemekezedwa (Kwa 
Mulungu); 

14. Apamwamba ndiponso 
oyeretsedwa (Kumbiri iliyonse 
yopunguka); 

15. Omwe ali m'manja mwa 
Alembi (Angelo). 

16. Olemekezeka, omvera. 

17. Waonongedwa 
(watembereredwa) Munthu. 
Mkwanji kusayamika Kwake 
kotereku. 

18. Kuchokera mchinthu chanji 
Chimene iye adamulenga. 

19. Kuchokera kumadzi 
(opanda pake) Adamulenga, 
namkonzeratu mkalengedwe 
Kosiyanasiyana. 

20. Kenako adamfewetsera njira 
(Yotulukira m'mimba mwa mai 
ake). 

21. Ndipo amamchititsa kuti 
Amwalire namukumbila manda, 

22. Kenako akadzafuna 
adzamuukitsa (Pambuyo pa imfa). 

23. Ayi ndithu (munthu) 
sanakwaniritsebe Zimene 



@tf 



tfjOMiiy 



c^ 3 






I ^<3^i$ 






Surat 80, 'Abasa Juzu 30 1326 ? * *& 



A * ,j~* 5 j>^ 



adamulamula Mbuye wake 
(Mulungu chingakhale Wakhala 
nthawi yaitali padziko Lapansi). 

24. Alingalire munthu (mmene 
chilili) Chakudya chake; 1 

25. Ndithu, Ife timagwetsa 
mvula Yambiri (kuchokera ku 
mitambo). 

26. Kenako timaing'amba 
nthaka kuti Mmera utuluke; 

27. Ndipo timameretsa 
m'menemo njere (ya Chakudya 
cha anthu ndi zina Zimene 
amasunga kunkhokwe), 

28. Ndi mphesa ndi msipu. 

29. Ndi mzitona (wabwino) ndi 
(Zipatso za) kanjedza, 

30. Ndi minda yothothana 
nthambi Za mitengo, 

31. Ndi zipatso (zodyedwa ndi 
anthu) Ndi msipu (wodyedwa ndi 
nyama); 

32. (Tazimeretsa zimenezo kuti) 
Zikondweretse inu ndi ziweto 
Zanu. 

33. Ndipo likadzafika lipenga 
Logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa 
Makosi). 









b\&?$&\i 






^<&%'g% 









&&±%ptiz 



©<tLik)l^Cl3b 



1 Ngati munthu sakumbuka chilengedwe chake, ayang'ane chakudya chimene 
akudya momwe chimapezekera. Azindikira mphamvu za Mulungu. 



Surat 80. 'Abasa 



Juzu 30 



1327 



r* fijk-\ 



A * ^p-P 9jJ~> 



34. Patsikuli munthu adzathawa 
m'bale Wake, 

35. Mayi wake ndi bambo wake, 

36. Mkazi wake ndi ana ake. 

37. Munthu aliyense mwa iwo, 
tsiku Limenelo adzakhala ndi 
zakezake Zotangwanika nazo. 
(Sadzalabadira Za anzake). 

38. Tsiku limenelo nkhope zina 
Zidzakhala zowala; 1 

39. Zosekelera ndi 
zachimwemwe (Chifukwa cha 
nkhani yabwino ya Kumunda wa 
mtendere.) 

40. Ndipo nkhope zina tsiku 
limenelo Zidzakhala zokutidwa ndi 
fumbi. 

41. Mdima udzadzikuta. 

42. Iwo ndi anthu 
osakhulupirira Oipa (olakwira 
Mulungu). 



* A 9 • 9 .& 






&&&L& 



y(k'"t<'9f - '9&*9999' 






1 (Ndime 38-39) Tsiku limenelo anthu adzakhala kakhalidwe ka mitundu iwiri: 
amene adakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino nkhope zawo zidzawala 
ndi chimwemwe, ndipo amene adakanira ndikumachita zoipa, nkhope zawo 
zidzakhala zafumbi ndi zakuda monga momwe anenera ma aya 40 ndi 42. 



Surat 81. At-Takwir Juzu 30 



1328 



r. *>» 



A > jjj^sll 5 jj-» 



SURAT AT-TAKWIR LXXXI 





Surayi ikupereka chithunzithunzi chammene zinthu 
zidzakhalira kumayambiriro kwa tsiku la Kiyama ndi pambuyo 
pake. Ndipo yasonyeza maonekedwe amphamvu zake 
ndikutsimikiza ulemerero wa Qur'an ndikumuyeretsa Mtumiki 
ku misala imene amamganizira nayo. Ndipo yawaopseza 
opitiriza kusokera, ndikunenetsa kuti mQur'an muli maphunziro 
othandiza kwa anthu olungama. 



Surat At-Takwir LXXXI 



r 



^J^^ ^^2^^_y^\ 



V&m$] 



' .-re- i$cv? 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Pamene dzuwa 
lidzakulungidwe (Ndikuchotsedwa 
kuwalakwake), 1 

2. Ndi pamene nyenyezi 
zidzathothoke (Ndi kuchoka 
dangalira Lake), 

3. Ndi pamene mapiri 
adzayendetsedwe (Kuchoka 
mmalo mwake), 2 

4. Ndi pamene ngamira zabere 
Lamiyezi khumi zidzasiidwe 
(Zopanda oziyanga'anira), 3 



o^l^jll^U- 



-^ 









m 



%a&xj^m 



1 Surah zambiri zimene zidavumbulutsidwa ku Makka zimanena zododometsa 
za tsiku lomaliza. Kuyambira ayah iyi mpaka kudzafika ayah 14 Mulungu 
watchula zina zododometsa za tsiku lomaliza. 

2 Tsiku limenelo mapiri adzakhala osalimba ngati thonje limene likungouluka 
ndi mphepo. 

3 Ngamira za bere ndi chuma cha mtengo wapatali kwa Aarabu. Akuuzidwa 
apa kuti tsiku limenelo adzazisiya osalabadira konse. 



Surat 81. At-Takwir Juzu 30 



1329 



»>' 



A> jlj&^\ *jj-» 



5. Ndi pamene nyama za 
mtchire Zidzasonkhanitsidwe 
pamodzi (kuchokera mmalo 
osiyanasiyana Chifiikwa 
chakuopsa kwakukulu kwa 
Tsikulo), 1 

6. Ndi pamene nyanja 
zidzayatsidwe Moto, 

7. Ndi pamene mizimu 
idzalumikizidwe (Ndi matupi ake) ? 

8. Ndi pamene mwana wamkazi 
yemwe Adaikidwa m'manda 
wamoyo Adzafunsidwe, 2 

9. Ndi tchimo lanji adaphedwera? 

10. Ndi pamene makalata 
(mom we Mudalembedwa zochita 
za aliyense) Adzatambasulidwe 
ndi kugawidwa (Kuti 
awerengedwe), 3 

11. Ndi pamene thambo 
lidzayalulidwe (Kuchoka mmalo 
mwake), 



$&y£(j*£y\\&5 






©(s^CA9*a!lbb 



af<£&r&i!llSi; 



mtchire 



Mwa zina zododometsa pa tsiku limenelo ndi nyama za 
kusonkhanitsidwa pamodzi popanda kumenyana kapena kudyana. 

2 (Ndime 8-9) Ma ayah awiriwa akufotokoza momwe Aarabu adaiili Usilamu 
usadabwere. Munthu ankati akapatsidwa mphatso ya mwana wa mkazi adali 
kukhumudwa ndi kudandaula kwambiri. Ankanena kuti asungwana ngopanda 
phindu ndipo kuti kudali kuononga zinthu pakumulera , kumudyetsa, ndi 
kumuveka. Ndipo akadzakhala wachiwerewere adzakhala manyazi aakulu 
kwa makolo ake. Pamene chidadza chisilamu chidathetsa mkhalidwewu. 
Ndipo apa Mulungu akutisonyeza kuti patsiku limenelo, la chiweruzo, mwana 
uja adaikidwa wa moyo, adzafunsidwa kuti adaphedwa ndi tchimo lanji. lye 
adzayankha kuti sadachite tchimo lililonse koma adaphedwa mopanda 
chilungamo. 

3 Awa ndi makalata achiwerengero momwe mwalembedwa zabwino za 
munthu ndi zoipa zake. Tsiku limenelo munthu aliyense adzapatsidwa yake 
kalata kuti aone iye mwini zoipa ndi zabwino zake. 



Surat 81. At-Takwir Juzu 30 



1330 



*>' 



A 1 jt£d\ 5j>-» 



12. Ndi pamene Jahena 
idzasonkhezeredwe 
Mwamphamvu, 1 

13. Ndi pamene Jannah 
idzayandikitsidwe, 

14. (Zikadzachitika zimenezi) 
mzimu Uliwonse udzadziwa 
zimene Wabweretsa (zabwino ndi 
zoipa). 

15. Ndikulumbirira nyenyezi 
zimene Zimabwerera masana ndi 
kutulukanso Usiku. 

16. Zomwe zimayenda kenako 
nkubisika, 

17. Ndi usiku pamene ukulowa. 

18. Ndi m'mawa kukamacha; 

19. Ndithu iyi (Qur'an) ndi liwu 
la mthenga Wa Mulungu (Jibril) 
wolemekezeka (kwa lye), 

20. Mwini mphamvu ndi mwini 
ulemelero Kwa Mwini Mpando wa 
chifumu, 

21. Womveredwa kumeneko 
ndiponso Wokhulupirika 
(pachi vumbulutso) . 












1 (Ndime12-13) Tsiku limenelo Jannah idzayandikitsidwa kwa ochita zabwino 
ndiponso moto udzayandikitsidwa kwa ochita zoipa kuti aone kumalo kwake. 

2 (Ndime 19-20) Mthenga wolemekezeka womveredwa uko kumwamba ndi 
Jibril (Gabriel) yemwe ndi wamkulu wa angelo onse. lye ndiyemwe adali 
kubweretsa Qur'an mwa lamulo la Mulungu kwa Mneneri Wake Muhammad 
(SAW). Ndipo ulemelero wa Qur'an ndi ulemelero wa Mneneri (SAW) 
chifukwa choti munthu wolemekezeka amamutumizira mthenga 
wolemekezeka. Ndipo uthenga wabwino umapatsidwa kwa Mneneri wabwino 
woposa onse. 



Surat 81. At-Takwir Juzu 30 



1331 



f » f,j)r\ A ) jij^sll ijj*t 



22. Ndipo m'bale wanu uyu 
siwamisalaayi. 1 

23. Ndithu, ndikulumbira kuti 
(iye Mtumiki) (SAW) Adamuona 
(Jibril) mchizimezime 
(chakum'mawa) Chooneka bwino. 

24. Ndipo sali iye (Mtumiki) 
waumbombo Ndi chivumbulutso 
(koma amafikitsa zonse 
Ndikuziphunzitsa kwa anthu). 

25. (Chivumbulutso chomwe 
chavumbulutsidwachi Kwa iye) si 
mawu a satana wothamangitsidwa 
Mchifundo cha Mulungu; 

26. Nanga mukupita kuti? 

27. (Qur'ani) iyi sichina koma 
Ndi chikumbutso cha Zolengedwa 
zonse. 

28. Kwa yemwe mwa inu 
akufuna Kuyenda mu njira 
yoongoka. 

29. Ndipo simungafune chinthu 
mwa Inu nokha pokhapokha 
atafuna Mulungu Mbuye wa 
zolengedwa zonse. 












1 (Ndime 22-25) Anthu okanlra pamene adasowa chonena kwa mneneri 
(SAW) adali kunena nkhani zabodza kuti Mtumiki (SAW) wapenga ndikuti 
zomwe akulankhula sadapatsidwe ndi Jibril, 



Surat 82. Al-Infitar Juzu 30 



1332 



**\ 



AT jlkiW 5j>-» 




Surayi yasonyeza zina mwazoopsa zimene zidzachitike tsiku 
la Kiyama ndi malankhulidwe osonyeza kuti zichitikadi 
posachedwa, patsiku limene munthu aliyense adzadziwa zimene 
adatsogoza ndi zomwe adazisiya. Kenako surayi yachenjeza 
munthu wonyengedwa pakusalabadira Mulungu wake amene 
adamlenga ndikumlinganiza bwino. Ndipo adampatsa 
maonekedwe abwino, olingana. Ndipo kenako yatsimikiza 
kukanira kwa munthu za tsiku la chiweruzo, ndikutsimikiza kuti 
munthu ali nawo angelo omwe akulemba chilichonse. Ndipo 
yatsatiza pankhaniyi kutchula za mtendere womwe anthu 
abwino adzapeza, ndiponso Jahena imene idzakhala ya anthu 
oipa; adzailowa pa tsiku la Kiyama lomwe ndi tsiku limene 
mzimu sudzakhala ndi mphamvu zothangatira mzimu wina. 
Ndipo zonse zidzakhala za Mulungu yekha. 



Surat Al-Infitar LXXXII 






I mm% 



■ ;?"}- 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Pamene thambo lidzasweke, 1 

2. Ndi pamene nyenyezi 
zidzayoyoke (Ndi kumwazikana), 

3. Pamenenso nyanja 
zikuluzikulu Zidzaphwasulidwe. 

4. Ndiponso pamene manda 
Adzafukulidwe (ndikutuluka 
Akufa omwe adali mmenemo), 



o^i^JMkU. 






1 Kuyambira pa aya 1 mpaka 4, Mulungu akutisonyeza zododometsa zina za 
tsiku lomaliza. 



Surat 82. Al-Infitar Juzu 30 1333 r * *>» 



AT jlW}|1 5jj^» 



5. (Panthawiyo) mzimu 
uliwonse Udzadziwa zimene 
Udatsogoza (zabwino ndi zoipa) 
Ndi zimene udasiya m'mbuyo. 1 

6. E! Iwe munthu! Nchiani 
chakunyenga Kumsiya Mbuye wako 
wa ufulu (Kufikira pomnyoza)? 

7. Amene adalenga iwe 
Nakulinganiza (ziwalo zako) ndi 
Kukulongosola (moyenera); 

8. Ndipo maonekedwe amtundu 
Uliwonse omwe adawafuna 
Adakuveka (popanda chifuniro 
Chako). 

9. Ayi, sichoncho! Koma inu 
Mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro. 

10. Ndithu, pa inu alipo 
okuyang' anirani, 2 

11. Olemekezeka, olemba 
(zochita Zanu.) 

12. Akudziwa (zonse) zimene 
muchita (Zabwino ndi zoipa). 

13. Ndithudi ochita zabwino 
Adzakhala mumtendere. 

14. Ndipo ndithu, amene ali 
olakwira Malamulo a Mulungu 
adzakhala Ku moto wopsereza. 

15. Adzaulowa tsiku la malipiro. 






©(j^JJI 



^r^'ft? 



1 Munthu aliyense pa tsiku limenelo adzadziwa zimene adachita, zabwino ndi 
zoipa. 

2 Munthu aliyense ali nawo angelo awiri, Rakibu ndi / 
kulemba ntchito za munthu, zabwino ndi zoipa zomwe. 



zoipa. 

2 Munthu aliyense ali nawo angelo awiri, Rakibu ndi Atidu. Ntchito zawo ndi 



Surat 82. Al-Infitar Juzu 30 I 1334 T * *>i At jiWsM «j>- 



16. Ndipo iwo kumoto 
Sadzachokako. 

17. Kodi nchiyani 
chingakudziwitse za Tsiku la 
malipiro? 

18. Ndipo nchiyani 
chingakudziwitse za Tsiku la 
malipiro? 

19. Limeneli ndi tsiku limene 
mzimu Uliwonse sudzakhala ndi 
mphamvu (Yodzetsa mtendere 
kapena Yochotsa chovuta) pa 
mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku 
limeneli Ndi la Mulungu yekha. 1 










Surayi yayamba ndikulonjeza za chilango choopsa kwa 
amene akuphangira pamalonda; popatsa ena zosakwanira 
pamuyezo wake. Ndipo anthu amtundu uwu yawaopseza kuti 
adzauka mmanda ndikuwawerengera zochita zawo, ndipo 
yanenetsanso kuti ntchito zawo zikulembedwa mkaundula 
wowerengedwa malembo bwinobwino. 

Tsiku limenelo palibe angalikanire kupatula wopyola malire 
ndi wamachimo ambiri. Wotereyo sakamuona Mbuye wake. 
Ndipo kobwerera kwake ndi ku Jahena. 

Surayi yatchulanso za anthu abwino ndikuwatonthoza 
ndikuwapatsa chikhulupiriro cha kupambana pantchito zawo 
zabwino. Ndipo yafotokozanso zamtendere wawo ndikupambana 



Tanthauzo lake ndikuti tsiku limenelo sipadzakhala munthu wotha 
kumthandiza mnzake pa chilichonse ndiponso palibe adzakhale ndi mphamvu 
zolamula kupatula Mulungu yekha. 



Surat 83. Al-Mutaffifin Juzu 30 1335 T ♦ ^j*-i AT osiibli h**> 



kwawo. Kenako surayi yatipatsa chithunzithunzi chamomwe 
Akafiri ankawachitira Asilamu pamene ankaona Asilamu 
akuwadutsa. Surayi yamaliza ndikulongosola kuti naonso 
Asilamu adzabwezera chipongwe kwa Akafiri pa zomwe 
ankawachitira padziko lapansi. 



Surat At-Mutaffijln LXXIII 



r^^ 1 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuonongeka koopsa 
kukawapeza Opunguza miyezo ya 
malonda 

2. Amene amati Akamadziyezera 
zinthu kwa anthu amafuna 
Kulandira miyezo yodzadza. 

3. Koma pamene iwo 
akamawayezera pa Muyezo 
wambale kapena wa sikelo 
Amapungula (choyenera kulandira 
Ogulawo). 

4. Kodi amene akupungula 
miyezo Pamalondawo sakuganiza 
kuti Adzaukitsidwa; 

5. Pa tsiku lalikulu (ndiponso 
Loopsa)? 

6. Tsiku limene adzaimilira anthu 
Pamaso pa Mbuye wa zolengedwa. 

7. Ayi! Ndithu (siyani chinyengo 
Pamalonda ndi kusalabadira kuuka 
Mmanda); Zolembedwa za ntchito 
Ya oipa zili m'Sijjin. 



Q 



>^l<^5MkU- 



( %feWcS 



$&&jw#mw$ 






x '^^^jtef'iVfJi&if 






j&&j&&®x 



Surat 83. Al-Mutaffifin Juzu 30 



1336 



r» *>i 



AT ooilail Ojj-rf 



8. Nanga nchiyani 
chitakudziwitse Za Sijjin? 

9. Ameneyu ndi kaundula 
Wamkulu yemwe walembedwa 
(Mkati mwake ntchito za Anthu 
oipa). 

10. Chilango chaukali tsiku 
Limenelo chili pa otsutsa, 1 

11. Amene akutsutsa Za tsiku la 
malipiro. 

12. Ndipo palibe angalitsutse 
Koma yekhayo wopyola malire 
(Pochita zoipa); wa machimo 
Ambiri; 

13. Pamene ma ayah Athu 
akuwerengedwa kwa iye (onena za 
tsiku La malipiro ndikuuka 
mmanda) Amanena kuti "Izi ndi 
nthano Za anthu akale." 

14. Iyayi ? sichoncho! Koma 
Yaphimbidwa mitima yawo ndi 
Dzimbiri (la machimo) omwe 
Akhala akukolola. 2 



0<J^\i<^jSllj 



*J9>l?%9l K 









$®'f$&Q?($$ 



s>9 >6 



1 Kutsutsa kulipo kwa mitundu itatu: 

(a) Kutsutsa kwa mawu ndi zochita; 

(b) Kutsutsa kwa zochita zokha, monga ukauzidwa kuti chinthu ichi nchoipa, 
munthu nkudziwa kuti zoona nchoipadi koma nkudzachichita chimenecho 
mosalabadira; 

(c) Kutsutsa ndi zolankhula zokha. Kumeneko ndiko monga munthu akudziwa 
kuti chakutichakuti ncholetsedwa (haramu) koma m'malo mwake iye nkumati 
chimenecho nchovomerezeka (halali) 

2 Munthu akachita choipa koyamba ndipo osalapa, limalowa dontho lakuda 
mu mtima mwake; nthawi iliyonse pamene akuonjezera machimo, dontho lija 
limakulirakulira mpaka kuuphimba mtima wonse. Dontho limeneli ndilo 
likutchedwa "Ran." Tsono mtima ngati utaphimbidwa chotere sulabadira 
kuchita zoipa, ngakhale kuti auongole sungaongoke. 



Surat 83. Al-Mutaffifin Juzu 30 1337 T • >>» AT &M\ oj^ 



15. Ayi ndithu iwo (okanira) 
tsiku Limenelo) adzatchingidwa 
Kwa Mbuye wawo; (Sadzamuona). 

16. Pambuyo pake adzalowa ku 
Moto; (oyaka) 

17. Kenaka adzauzidwa 
(Powaliritsa) "Ichi Ndi chilango 
chomwe Mudali kuchitsutsa (pa 
dziko Lapansi)." 

18. Zoona, ndithu, kaundula wa 
Anthu abwino (ochita ntchito 
Zabwino) ali mu Illiyyun. 

19. Nanga nchiyani 
chitakudziwitse za Illiyyun? 

20. Ameneyu ndi kaundula 
(wamkulu) Yemwe walembedwa 
(mkati mwake Ntchito za anthu 
abwino); 

21. Amamuyikira umboni 
(angelo) Amene ayandikitsidwa 
(kwa Mulungu). 

22. Ndithu, ochita zabwino 
Adzakhala mu mtendere, 

23. Atakhala pa mipando ya 
ulemu Uku akuyang'ana (zimene 
Mulungu wawapatsa monga 
Mtendere ndi ulemerero). 

24. Udzaona kuwala kwa 
mtendere Pa nkhope zawo; 

25. Adzamwetsedwa vinyo 
(woyeretsedwa) Wotsekeredwa ndi 
zitsekero Zolimba; 






b '29*9 9' 









Surat 83. Al-Mutaffifin Juzu 30 1338 r * *>» 



AT ONtfkit 5jj-- 



26. Komalizira kwake (kwa 
vinyoyo) Kuzikatuluka fungo la 
misk; Kuti akapeze zimenezi, 
apikisane Opikisana. 1 

27. Ndipo chosakanizira cha 
Vinyoyo ndi madzi a Tasnim. 

28. (Tasnim ameneyo) ndi 
kasupe Amene azikamwa amene 
ayandikitsidwa (Kwa Mulungu.) 

29. Ndithu, amene adachita 
machimo Adali kuwaseka 
(mwachipongwe) Okhulupirira 
(padziko lapansi); 

30. (Okhulupirira) Akadutsa 
pafupi ndi iwo Ankakodolerana 
maso (Mwachipongwe); 

31. Ndipo akabwerera kwa 
anzawo Amabwerera akusangalala 
(Ndi kunyozedwa kwa 
okhulupirira); 

32. Ndipo (nthawi zonse) 
akawaona Asilamu amanena: 
"Ndithu, awa Ndi osokera 
(chifukwa chomkhulupirira 
Mtumiki)." (SAW) 

33. Sanatumizidwe (Akafiri) 
kukhala Ayang'aniri kwa 
okhulupirira (Ndikuwaweruza 
zakulungama ndi Kusokera). 

1 Apa, akutilamula kupikisana pakuchita zabwino kuti tipeze madalitso amene 
awakonzera anthu abwino. Kumeneko ndikuti munthu aliyense alimbikire 
kuchita mapemphero ndi zina zabwino. 



(J&&£$X&&Z*®r 



©(j ^ «»jl:J J\ 


















®<<M^ 



0(1$ wJ 



e ®&^4Jfc 



Surat 83. Al-Mutaffifin Juzu 30 



1339 



*>' 



fs? j^ilail 5jj-*» 



34. Basi patsikulo okhulupirira 
adzaseka Osakhulupirira 
(powabwezera chipongwe Chawo 
chimene ankachita padziko 
Lapansi), 1 

35. Atakhala pa mipando ya 
ulemu uku Akuyang'ana 
(mtendere umene Mulungu 
Wawapatsa). 

36. Kodi alipidwa 
osakhulupirira Pazomwe ankachita 
zija (padziko Lapansi)? 



iS&i«5*ijft&A3& 



l" " 



®£n4®&- 



© (j^l^ly^^j^lo^^ 




Surayi yalongosola zina mwazisonyezo za Kiyama ndikuti 
nthaka ndi thambo zidzagonjera zofuna za Mulungu. Ndikutinso 
munthu adzakumana ndi Mbuye wake Mulungu. Ndikutinso 
zochita zake zikulembedwa m'buku limene adzaliona 
ndikulilandira. Amene adzalirandire ndi dzanja lamanja, ndiye 
kuti chiwerengero chake chidzakhala chofewa, pomwe amene 
adzalirandire ndi dzanja la kumanzere ndiye kuti adzalira 
kwambiri kuopa kukumana ndi chilango chamoto. 

Kenako Mulungu walumbirira zoonekera mwazisonyezo 
Zake zomwe zikuikira umboni mphamvu Yake,ndikuitanira ku 
chikhulupiriro cha kuuka kwa akufa. Koma ngakhale zili 
chonchi, anthu okanira sakhulupirira ndi kulingalira Qur'an 
ndikugonjera malamulo ake. 

Surayi yamaliza ndi kuopseza kuti Mulungu akudziwa 



1 (Ndime 34-36) Tanthauzo lake ndikuti okhulupirira, tsiku lomaliza adzakhala 
m'mipando ya ulemu uku akuwayang'ana ndi kuwaseka anthu osakhulupirira 
ali m'mavuto monga momwe iwo adali kuseka okhulupirira pa dziko lapansi. 



Surat 84. Al-Inshiqaq Juzu 30 1340 I T • *>» At JlLSJ* 5jj- 



zimene akubisa mmitima mwawo. Ndipo wawakonzera chilango 
chowawa. Chimodzimodzinso kwa okhulupirira, wawakonzera 
mphoto yokoma yamuyaya. 



Surat Al-Inshiqaq LXXXIV 



w%tf: 



\mm&^ym 



OJj*&\uP&\fr\j>. 



-& 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Pamene thambo 
lidzang'ambike (Kusonyeza 
mapeto ake), 

2. Ndikudzamvera lamulo la 
Mbuye Wake; ndipo lidzayenera 
kutero, 

3. Ndiponso pamene nthaka 
Idzatambasulidwe (pogumuka 
Mapiri ake ndikuchoka zitunda 
zake), 

4. Ndi kutaya zomwe zidali 
mkati Mwake ndi kukhala 
Yopandakanthu, 1 

5. Ndikudzamvera lamulo la 
Mbuye Wake; ndipo lidzayenera 
kutero. (Choncho Zikadzachitika 
zimenezi ndiye kuti munthu 
Adzalandira mphoto ya zochita 
zake). 2 



1 Chimodzi mwa zinthu zoopsa zomwe zidzachitika tsiku lomaliza ndi 
kugwedezeka kwa nthaka mwamphamvu zedi mpaka idzalekana ndi mapiri 
amene ali zichiri zake zoletsa kugwedezeka kwake. Pachifukwa ichi 
idzatambasuka ndipo zomwe zidali mkati mwake zidzatulukira pamtunda; 
nthaka idzangokhala yopanda kanthu mkati mwake. 

2 Ambuye Mulungu pambuyo ponena zimenezi sadanene kuti chidzachitika 



&£B\jfc3\\k 












©<c*£>^ \& y J, <c* $j 



Surat 84. Al-Inshiqaq Juzu 30 1341 r • *>■! At JUL^i Sj^ 



6. E! I we Munthu! Ndithudi iwe 
Ukubwerera kwa Mbuye wako 
(ndi Zochita zako zabwino kapena 
Zoipa), kubwerera kotsimikizika, 
Ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira 
Za zochitachita zako). 

7. Tsono amene adzapatsidwe 
kaundula Wa zochita zake 
kudzanja La manja, 1 

8. Basi iye, adzawerengedwa, 
Kuwerengedwa kopepuka, 2 

9. Ndipo adzabwerera kwa anthu 
ake (Okhulupirira) ali wokondwa. 

10. Koma yemwe adzapatsidwe 
kaundula Wa zochita zake 
chakumanzere Kudzera kumbuyo 
kwa msana wake (Chifukwa 
chomunyoza), 

11. Basi, iye adzaitana imfa 
(kuti Imufikire; kuti afe apumule, 
Koma siidzamufikira); 

12. Ndipo adzalowa ku moto 
woyaka. 






i^JC^&W 









®\%?«<^*l$ 



chiyani. Alekera munthu mwini wake kuti aganizire chomwe chidzachltika 
zikadzapezeka zoopsa kuti aope kwambiri. 

1 Tsiku la chiweruzo munthu adzapatsidwa kaundula wake monga momwe 
zanenedwa mu ayah 10 Surah Takwir, choncho ena adzapatsidwa ndi dzanja 
la kumanja; iwo ndiwo anthu abwino. Pomwe ena adzapatsidwa ndi dzanja la 
kumanzere, chakumbali yakumsana; iwowo ndiwo anthu oipa. 

2 Anthu ena adzawerengedwa popanda kufunsidwa mafunso pa zimene 
adachita, koma adzangowauza zabwino zawo ndi zoipa zawo ndipo pambuyo 
pake adzawakhululukira zoipazo ndi kudzawalipira pa zabwinozo. Iwowa ndiwo 
anthu abwino; chimenechi ndicho chiweruzo chofewa. Ena adzaweruzidwa 
pofunsidwa pa chilichonse m'zimene ankachita monga kuti "Bwanji ichi 
udachita? Bwanji ichi sudachite"? Iwowa ndiwo anthu oipa; chiwerengero 
chawo chidzakhala chokhwima. 



Surat 84. Al-Inshiqaq Juzu 30 1342 T * *>» At JU^j^i Sj>- 



13. Kamba kakuti iye adali 
wokondwa; (Kukondwa kwa 
machimo) pamodzi Ndi anthu ake 
(osaganizira za Mathero ake). 

14. Ndithudi,amaganiza kuti 
Sadzabwerera (kwa Mulungu 
ndiponso Sadzawerengedwa). 

15. Chifukwa ninji 
(asabwerere)? Mbuye wake adali 
kumuona. (Choncho alipidwa 
zimene adachita). 

16. Ndikulumbirira kufiira Kwa 
dzuwa (pamene likulowa). 

17. Ndi usiku ndi zimene 
wasonkhanitsa, 1 

18. Ndi mwezi ukakwanira 
dangalira (Lake), 

19. Ndithudi mudzachoka apa 
kunka apa (Pa umoyo uno 
mpakana Umene uli nkudza). 

20. Kodi nchiyani chikuwaletsa 
iwo (Okanira) kukhulupirira 
(Mulungu Ndi kuuka kumanda, 
zisonyezo zake Zitaonekera 
poyera)? 

21. Ndipo ikawerengedwa kwa 
iwo Qur'an, Sagwetsa pansi 
nkhope zawo (Modzichepetsa). 






®, 






s ^mo$^&& 



1 Kubalalikana masana ndi chizolowezi cha anthu ndi nyama chifukwa 
chofunafuna zinthu zothandiza pa moyo wawo. Tsono usiku ukabwera 
amasonkhana ndi kukhala pamodzi. Ndipo ili ndilo tanthauzo la "usiku ndi 
zimene wasonkhanitsa." 



Surat 84. Al-Inshiqaq Juzu 30 1343 r • *>» At JUjysh oj^- 



22. Koma amene 
sadakhulupirire Akutsutsa basi 
(chifukwa cha Makani ndi 
kudzikweza). 

23. Ndipo Mulungu akudziwa 
(bwinobwino) Zimene 
akuzisonkhanitsa. 

24. Choncho, auze nkhani 
Yachilango chopweteka. 

25. Kupatula awo amene 
Akhulupirira ndikuchita Ntchito 
zabwino, kwa iwo Kuli malipiro 
osatha. 1 



®*m&&M 






,r .' ' 



Z. 9 9s'99'^>'\99\ 




SURAT BURU J LXXXV 




M'surayi muli mawu omutonthoza Mtumiki ndikuwakumbutsa 
Asilamu, ndiponso kuopseza ndi chilango kwa osakhulupirira. 
Yayamba ndikulumbirira kwa Mulungu pa zisonyezo zosonyeza 
mphamvu yake ndi luso lake lakuya pa chilichonse potsimikiza 
kuti amene akuzunza okhulupirira adzathamangitsidwa kubwalo 
la chifundo Chake, monga momwe adathamangitsidwira ochita 
zoterezi mwa anthu akale. Ndipo surayi yalongosola za anthu 
oipa ndi zimene adali kuwachitira okhulupirira. Yalongosolanso 
kuti nthawi zonse choona chimathiridwa nkhondo ndi anthu 
oipa. Ndipo yamalizira kunena kuti Qur'an ndi mawu oona; 
mulibe chikaiko mkati mwake. Chifukwa idachokera m'buku 
lotchedwa "Lauhi Mahfudhi" lomwe lili kwa Mulungu. 



1 Ayah iyi ikusonyeza kuti kukhulupirira kokha sikungampulumutse munthu ku 
chilango cha tsiku lomaliza, koma nkofunikanso kuchita ntchito zabwino; 
m'Qur'an paliponse pamene akutchula za chikhulupiriro akutchulanso za 
kuchita ntchito zabwino. 



SOrat 85. Al-Buruj Juzu 30 1344 



►J*"' 



A© KJJ^\ ^j-j 



Surat Al-Buruj LXXXV 



' i$&£ ;*- 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira thambo 
lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi 
zikuluzikulu). 1 

2. Ndi tsiku lolonjezedwa 
(Kuwerengedwa ndi kulipidwa), 

3. Ndi woikira umboni, ndi 
woikiridwa umboni. 2 

4. Atembereredwa eni ngalande 
(mayenje) zamoto (Zomwe adali 
kuwazunzira okhulupirira 
Mulungu, Achimuna ndi 
achikazi). 3 

5. (Ngalande) za moto 
wankhuni (zambiri zomwe Adali 



o^t^^U. 



-^ 






**#LylS<AM 



1 Buruj ndi nyenyezi zomwe zimakhala m'magulumagulu ndipo gulu lililonse 
limatchedwa Buruj. Ndipo Buruj zonse zilipo khumi ndi ziwiri (12). Zisanu ndi 
imodzi zili kumpoto kwa "Equator", pomwe zisanu ndi imodzi zili kumwera kwake. 

2 "Woikira umboni ndi woikiridwa umboni" angathe kukhala aliyense woikira 
umboni ndi woikiridwa umboni pa tsiku lomaliza, monga aneneri adzaikira 
umboni anthu pa zabwino kapena zoipa; pa malo pochitira mapemphero 
padzamuikira umboni wazabwino yemwe adali kupempherapo. Ndipo pamalo 
pomwe padali kuchitikira zoipa padzawachitira umboni anthu oipa za 
machimo awo: ngakhale ziwalo ndi khungu nazonso pa tsiku limenelo 
zidzaikira umboni kwa mwini ziwalozo. Basi munthu akatsimikiza kuchita 
machimo akumbukire kuti ali nazo mboni zambiri zomwe zikumuona ndipo pa 
tsiku la chiweruzo zidzaima pa maso pa Mulungu kupereka umboni wokhudza 
munthuyo. 

3 Pamene Ayuda a ku Najrani adalowa m'Chikhristu, (Chisilamu chisadafike 
ndiponso Chikhristu chisadaonongeke), idamufika nkhaniyi mfumu yawo dzina 
lake Dhu-Nuwas; adabwera ku Najrani ndi gulu lankhondo lalikulu; 
adawakakamizira anthu ku Chiyuda koma iwo adakana. Nayamba kuwapha 
anthu okhulupirirawo powaponya m'ngalande za moto. 



Surat 85. Al-Buruj Juzu 30 1345 T * tjk-\ 



Ad j- jjt\ oj^ 



kuzikoleza ndikuotchera 
okhulupirira), 

6. Pamene iwo adali chikhalire 
m'mphepete mwa Ngalande za 
moto. 

7. Uku iwo akuyang'ana zomwe 
amawachitira Okhulupirira, 
(pootchedwa ndi moto). 

8. Sadaone choipa chilichonse 
mwa iwo koma Chifukwa choti 
adakhulupirira Mulungu mwini 
Mphamvu zonse ndiponso mwini 
kuyamikidwa, 

9. Yemwe ufumu 
wakumwamba ndi pansi ndi Wake; 
ndipo Mulungu ndi mboni 
pachilichonse. 

10. Ndithu, amene ayesa 
mayeso okhulupirira achimuna Ndi 
achikazi (pa chipembedzo chawo 
ndi Mazunzo ndi chilango cha 
moto), pambuyo pake Osalapa 
(pazimenezi), adzalandira chilango 
cha Jahena Ndiponso chilango cha 
moto wopsereza, 1 

11. Ndithudi amene 
akhulupirira ndi kuchita ntchito 
Zabwino, adzakhala ndi minda, 
(mom we) mitsinje Ikuyenda pansi 



&>j&&&>\ 


















1 Tanthauzo la "kuwazunza" apa ndiko kuwavutitsa ndi kuwathetsa mphamvu 
kuti asiye chikhulupiriro chawo; asakhulupirire mwa Mulungu. Mawuwa 
ngakhale akukhudzana ndi eni mayenje a moto, akukhudzanso akafiri a 
m'Makka omwe adali kuzunza Asilamu ndi mazunzo osiyanasiyana kuti 
abwerere kuchipembedzo cha mafano. Ndipo zimenezi zikhudzanso aliyense 



Surat 85. AI-Buriij Juzu 30 



1346 



r% *j*-i 



Ao r jjJl *JJ~*' 



pake; kumeneko ndiko 
Kupambana kwakukulu. 

12. Ndithu, kulanga kwa Mbuye 
wako (kwa Anthu achinyengo), ndi 
kwaukali kwambiri . l 

13. lye, (mmodzi yekha) ndi 
amene Adayambitsa zolengedwa 
ndiponso Ndi yemwe adzazibweze 
(pambuyo Poonongeka); 

14. lye, ndi Wokhululuka (kwa 
amene Walapa kwa lye), ndiponso 
Wokonda Kwambiri (amene 
akumkonda ndi Kumumvera), 

15. Mwini mpando wachifumu, 
(ndiponso) Wolemekezeka 
(mmene alili ndi Mbiri Zake), 

16. Wochita zimene wafuna, 
(ndipo Chimene wafuna 
sichikanika). 

17. Kodi yakufika nkhani ya 
magulu a nkhondo, 



©L)J^^jJ^(ji 






1 (Ndime 12-16) Ambuye Mulungu pambuyo powatonthoza Asilamu 
pakuwauza zomwe zidawaonekera abale awo amene adatsogola, tsopanonso 
akuwatonthoza ndi ufumu Wake wolemekezeka kuti adziwe kuti awo akafiri 
omwe akudziona kuti ali ndi mphamvu zolangira anzawo, lye sangamuthe. 
Akafuna adzawalanga ndi chilango cha dziko lapansi ndi cha tsiku lomaliza, 
kapena chimodzi mwa zilangozi; pakuti lye Ngokhululuka kwambiri ndiponso 
Ngwachikondi zedi, awatembenula mitima yawo kuti achikhulupirire chimene 
adachikana. Chifukwa cha mphamvu Zake zoposa, Mulungu, adachita 
zonsezi ziwiri. Patapita zaka zochepa adawapatsa mphamvu omwe adali 
opanda mphamvu, kenaka adayamba kuwalanga osakhulupirira aja chilango 
cha padziko, monga Abu Jahl ndi anzake omwe adali kumutsutsa kwambiri 
Mtumiki (SAW) pamodzi ndi omutsatira ake. Ndipo ena adawatembenula 
mitima yawo nkulowa mchipembedzo cha Chisilamu; adaima ndikuchiteteza 
Chisilamu popereka nsembe ya mizimu yawo ndi chuma chawo. 



Surat 85. Al-Buruj Juzu 30 1347 T * *>i 



A 6 £Jj$\ *JJ~* 



18. Firiaun (Farao) ndi Samudu, 
(Ndi chilango chimene 
chidawapeza Chifukwa 
chakulimbikira kwawo pa Zinthu 
zopanda pake)? 

19. Koma amene 
sadakhulupirire ali Mkati motsutsa 
basi. 

20. Koma Mulungu awazinga 
mbali Zonse. 

21. Koma iyi ndi Qur'an 
yolemekezeka. 

22. Yomwe idachokera mu 
ubawo (Chisileti chachikulu) 
wotetezedwa (Ndi manja alionse, 
osintha kanthu Kapena 
kuonjezerapo). 



h S9f' ' S9'9. 

>j+>) vjP-j} 



®^My&&#\& 



m&$&M 









a;;: ■ . 



SURAT AT-TARIQ LXXXVI I'j^^ff 

Js^fe"! 1 k „;_ „^-~- ^P^Jll& 

Surayi yayamba ndi kulumbirira nyenyezi zowala kwambiri 
zomwe zikusonyeza mphamvu ya Mulungu pachilichonse. 
Ndipo surayi ikutitsimikizira kuti aliyense alinaye msungi 
wake.Ndiponso ikumulangiza munthu kuti aganizire za kubadwa 
ndi kukula kwake, ndikuti adziwe kuti adalengedwa kuchokera 
kumadzi ofwamphuka kuti potero apeze zizindikiro zoti amene 
adamlenga kuchokera ku madzi,sangalephere kumuukitsa 
kuchokera mmanda. 

Ikulumbiriranso kuti Qur'an ndi mawu olekanitsa pakati pa 
choona ndi chonama. Koma akafiri akuikanira ndikuitchera 
misampha ngakhale ili choncho. Nayenso Mulungu wabwezera 
misampha yakuti ikawagwetse ku chionongeko chomwe 



Surat 86. At-Tariq Juzu 30 1348 T * *>» 



An JjUail djj** 



chidzakhala malipiro a kukanira ndi makani awo. Ndipo surai 
ikumuwuzanso Mneneri (SAW) kuti awalekerere Akafiri mpaka 
pomwe Mulungu adzaona chochita nawo. 



Surat At-Tariq LXXXVI 



,'iV*^ T ,'V'V 



= "r^ = 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira ku mwamba 
ndi Nyenyezi imene imadza usiku, 

2. Chitakudziwitse nchiyani za 
Nyenyezi yodza usikuyo? 

3. Imeneyo ndi nyenyezi 
yowala kwambiri (mu mdima). 

4. Ndithudi palibe mzimu 
uliwonse koma uli ndi msungi 
Wake (amene akuuyang'anira 
Ndikulemba zonse zochita zake). 

5. Aganizire munthu, kodi 
adalengedwa Kuchokera 
kuchiyani? 

6. Adalengedwa kuchokera ku 
Madzi ofwamphuka. 

7. Amatuluka kuchokera pakati 
pa Mafupa a msana ndi chifuwa (A 
munthu wa mwamuna ndi mkazi). 

8. Ndithujye ndiwakutha, 
Kum'bwezeranso (ku moyo 
pambuyo paimfa). 

9. Tsiku limene zobisika zonse 
Zidzaonekera poyera. 



Wtz mm&T<m 



o£g\<£&\A\j 



-^ 



6&mXi2\i 



©&j^<*Ly;i% 






^^\&&m 



&fik&&$ 



&&&&?£ 



Surat 86. At-Tariq Juzu 30 1349 T * ^jJfe-i A\ JjlWi 5^ 



10. Munthu sadzakhala ndi 
mphamvu (Tsiku limenelo 
zodzitetezera lye mwini) ndiponso 
sadzakhala Ndi mtetezi. 

11. Ndikulumbiriranso mitambo 
yobweretsabweretsa mvula. 

12. Ndi nthaka imene 
imang'ambika (Potulutsa m'mera), 

13. Ndithudi iyi (Qur'an) ndi 
mawu Olekanitsa (Haq ndi Batwili 
- Choona ndi chonama). 

14. Imeneyi sinkhambakamwa. 

15. Ndithudi iwo akukonza 
Chiwembu. 1 

16. Nanenso ndikuwakonzera 
Chiwembu (champhamvu 
kwambiri Chimene sangathe 
kuchipewa). 

17. Basi, apatse nthawi 
Osakhulupirira apatse Nthawi 
pang'ono, (aona posachedwa). 



&v$to&&*m 









©l^I^j 



©I^J^^t(^^(^6p 



1 (Ndime15-16) Tanthauzo lake ndikuti akafiri (osakhulupirira) akuchita ndale 
kuti azimitse dangalira la Qur'an ndikuyesetsa kuti awabweze amene 
adakhulupirira ndiponso ndikufuna kumupha Mneneri (SAW). Naye Mulungu 
akuwach'itira ndale powaonongera ziwembu zawo zomwe amaz'ikonza. 



Surat 87. Al-A'la Juzu 30 1350 T • >>» 



AV JIp^I 5j>- 




SURAT AL-A'LA LXXXVII 




wmm§ 



Surayi yayamba ndikulemekeza Mulungu amene adalenga 
zinthu ndikuzichita kukhala zofanana mkalengedwe. Ndipo 
chilichonse adachipatsa zoyenera zake ndikuchiongolera 
kuzimenezo. Adameretsa mmera, ndipo kenako nkuuchita 
kukhala wouma ndi wodera. 

Kenako surayi yanena kuti ndithu, Mulungu 
amamuwerengera Qur'an Mneneri Wake. Ndipo aloweza mu 
mtima mwake chowerengacho; saiwala chilichonse kupatula 
chimene wafuna lye mwini Mulungu. Ndipo amufewetsera 
kuchita zinthu zabwino. 

Kenakanso surayi ikulamula Mtumiki kuti awakumbutse 
amene akuopa Mulungu powalalikira Qur'an kuti akumbukire 
ndi kuthandizidwa ndi ulalikiwo. Koma woipa, mwini mavuto, 
adzipatula ku ulalikiwo. Ndipo akalowa ku moto waukulu. 

Surayi yatsimikiza kuti kupambana kuli kwa yemwe 
wayeretsa mtima wake ndikumakumbukira dzina la Mulungu 
uku akupemphera. Ndipo yamaliza ndikulongosola zimene 
zidalembedwa mmabuku akale, monga mabuku a Ibrahima ndi 
Musa. 



Surat Al-A <la LXXXVII 



M' dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Lemekeza dzina la Mbuye 
wako Wapamwambamwamba 
(ndikuliyeretsa Ku zinthu 
zosayenera). 1 






', •>;«■*; .: 



Q 



^i<*^U- 



-& 



^ C, $Jpl£ 



1 Tanthauzo lakulemekeza dzina la Mulungu ndiko kukhulupirira kuti lye 
ndiwopatulika ku mbiri zilizonse zolpa zosamuyenera, monga kumufaniza 



Surat 87. Al-A'la 



Juzu 30 



1351 



>>i 



AV J*H\ 5jj- 



2. Amene adalenga (chilichonse) 
Ndikuchikonza bwinobwino 
(Mkalengedwe kolingana); 

3. Amene adalamuliratu 
(chilichonse Zochita zake) ndi 
kuchiongolera; 1 

4. Ndi Yemwenso akumeretsa 
msipu; 

5. Ndipo nausandutsa kukhala 
wouma Ndi wodera. 

6. Tikulakatulira (chivumbulutso 
Chathu) ndipo suyiwala. 

7. Kupatula chimene wafuna 
Mulungu (Kuti uchiiwale); Ndithu, 
lye Amadziwa zoonekera ndi 
zimene Zimabisika. 

8. Ndipo tikufewetsera (njira 



*> \ '< ft? 



®(S3**3^(J$\ 









%aMWi 



ndizolengedwa; monga kuti anabereka kapena adaberekedwa, kapena kuti ali 
ndi mkazi kapenanso kuti alipo omwe amathandizana naye pa umulungu Wake. 

1 Mulungu pambuyo polenga zolengedwa Zake.sadangozileka kuti zisadziwe 
chochita, koma cholengedwa chilichonse adachilamuliratu kuti chichite 
zoyenera nacho, ndipo pambuyo pake adachiongolera pa chinthu 
chimenecho; chidadziwa, ndipo chidachita.Munthu a damusonyeza zomwe 
zili ndi mazunzo mkati mwake kuti adzitalikitse nazo ndiponso adamusonyeza 
zabwino kuti azichite. 

2 Mneneri Muhammad (SAW) adali munthu monga anthu ena ndipo adali ndi 
mbiri zonga anthu adalinazo, monga: kukonda ndi kusakonda, kuiwala ndi 
kukumbukira. Padapezeka kuti nthawi ina adaiwala ndi kupemphera maraka 
atatu m'swala ya maraka anayi. Pachifukwa ichi pa nthawi yovumbulutsidwa 
Qur'an ndi Jibril, adali akubwereza bwereza mawu ovumbulutsidwawo kuopa 
kuti angaiwale. Choncho, apa Mulungu akumuletsa kuti asadzivutitse 
kumabwerezabwereza mawuwo pamene akuvumbulutsidwa ndipo 
adamupatsa lonjezo nthawi yomweyo kuti sadzaiwala. Ndipo adakwaniritsa 
lonjezo Lake. Mtumiki (SAW) adali kumtsikira ma surah a ataliatali ndipo 
amatha kuwawerenga (molakatula) popanda kuonjezera kanthu kapena 
kuchepetsa, ngakhale kuti iye sadali kudziwa kuwerenga ndi kulemba. 
Kuwerenga kwake kudali kwakungolakatula pa mtima. 



Surat 87. AI-A< 



Juzu 30 



1352 



>>< 



AV J*H\ 5j>*> 



Yochitira zinthu) zabwino. 1 

9. Akumbutse (wanthu 
powalalikira) Ngati kukumbutsa 
kuthandiza. 2 

10. (Palibe chikaiko ulalikiwo) 
Aukumbukira (ndikuthandizidwa 
Nawo) amene akuopa Mulungu, 

11. Ndipo wamavuto ambiri, 
(Wamakani ndi wokanira), 
adzitalikitsa ndi ulalikiwo. 3 

12. Amene adzalowa ku moto 
waukulu (Umene wakonzedwa 
kuti udzakhale Malipiro ake); 



W*2vti& 



AWlM" 






1 Tanthauzo la 'kufewetsa' ndiko kuti Shariya ya Chisilamu (malamulo)siili 
yovuta kuyikwaniritsa monga momwe adalili malamulo a zipembedzo zoyamba. 
Ndipo ndi malamulo othandiza anthu onse, nthawi zonse ndi pamalo paliponse. 

2 Tanthauzo la apa sikuti Mtumiki (SAW) alalikire pokhapokha waona kuti 
ulalikiwo uthandiza ayi, koma alalikire ndithu kaya kulalikirako kuthandiza 
kapena ayi, monga momwe zalongosolera aya zotsatirazi. Kulankhula kotere, 
Arabu amakutcha "iktifa." 

3 "Wamavuto ambiri" apa, ndiko kuzunzika ndi matsoka. Mulungu akumutcha 
kafiri kuti "Wamavuto ambiri" chifukwa chakuti ali ndi mavuto padziko lino 
lapansi mpaka pa tsiku lomaliza. Mazunzo a tsiku lomaliza monga momwe 
tidziwira ndi chilango cha moto chomwe chikumuyembekeza. Tsono "chilango 
cha padziko lapansi" ndiko kuti alibe chinthu chomutonthoza likampeza tsoka 
kapena vuto lililonse. Msilamu likampeza vuto amadzitonthoza ndi chikhulupiriro 
chake chakuti moyo wa munthu suwonjezeka ndiponso suchepa, ndikuti 
munthu amamwalira akamaliza moyo wake. Koma kafiri saganiza choncho; 
amangokukuta zala ndi kuwatukwana ma dokotala kuti sadziwa kanthu 
akadachita mwakutimwakuti munthuyo sakadafa. Msilamu kukampeza kusauka 
amadzitonthoza ndi kupilira pamodzi ndi chikhulupiriro choti "chilichonse 
chimachitika mchifuniro cha Mulungu.," Ndipo amakhala woyembekezera kuti 
lero kapena mawa, Mulungu amupatsa chisomo Chake. Koma anthu opanda 
chikhulupiriro amangoona kuti aponderezedwa; amayetsetsa kufunafuna chuma 
mnjira zosayenera, ndipo akalephera amadzudzula uyu kapena kumenyana ndi 
uyu.ndipo amangodziona ngati wonyozeka kwambiri pa maso pa munthu wolemera. 
Kotero kuti atauzidwa kuti amulambire wolemera uja kuti amupatse 
ndalama,akhoza kuchita zotero. Ndipo tsiku lililonse njiru imamuondetsa; 
mwina amangodzipha monga momwe tionera masiku ano. Palibe mazunzo 
wakulu kuposa amenewa. Ngati muyang'ana ma ayah 16 ndi 17 muona kuti 
akuthirira umboni pa zimene talongosolazi. 



Surat 87. Al-A'la 



Juzu30| 1353 |r»*>t Mj*H\ijy* 



13. Ndipo sakafa m'menemo 
(ndikupumula kumazunzo), 
ndiponso Sakakhala ndi moyo 
(wamtendere). 

14. Ndithu, wapambana amene 
Wadziyeretsa (ku machimo), 1 

15. Ndikukumbukira dzina la 
Mbuye Wake (ndi mtima wake, ndi 
lirime Lake) uku akumapemphera. 

16. Koma inu mukonda 
kwambiri moyo Wa dziko lapansi, 

17. Pamene moyo wa tsiku 
lomaliza Ndi wabwino kwambiri 
ndiponso Wa muyaya. 

18. Ndithu, izi (mukuuzidwa 
m'Qur'an) Zilipo m'mabuku 
oyamba, akale, 

19. Mabuku a Ibrahim ndi Musa. 



*&8%&>Z& 



tfts&Fte 



®i^ip^% 






1 Tanthauzo lake ndikuti amene wadziyeretsa posiya kumuphatikiza Mulungu 
ndi zolengedwa ndi kumchimwira ndi machimo onse. Machimo amaletsa 
ulaliki wabwino kulowa mumtima wa munthu. (yang'anani ndemanga ya 14 
mu surat ya Mutaffifyn) 

2 Mawu akuti "wapambana amene wadziyeretsa ndi kumkumbukira Mbuye 
wake ndi kumapemphera", ndiponso kuti " tsiku lomaliza ndilabwino kuposa 
dziko lapansi" mawuwa adanenedwanso m'mabuku oyamba; sikuti Qur'an 
ndiyo yayamba kunena zimenezi. 



Surat 88. Al-Ghashiyah Juzu 30 



1354 



►J*-' 



A A 4-J»ttJl l^yM 



F 



WV #L ^SURAT AL GHASfflYAH LXXXVIH 

saga®^. 




Surayi yayamba ndi malankhulidwe okometsa mmakutu 
nkhani ya tsiku la Kiyama ndi zimene zidzachitike pa tsikulo. 
Ikulozera kuti tsikulo anthu adzakhala mmagulu awiri: gulu Una 
silikalandiridwa ndi ulemerero, ndipo likalowa ku moto 
wotentha, pomwe gulu lina likalandiridwa mwa chisangalalo ndi 
maonekedwe a mtendere omwe lidakonzedwera. 

Kenako surayi yatchula zisonyezo zoonekera poyera 
zosonyeza mphamvu ya Mulungu youkitsira anthu mmanda 
monga momwe akuonera ndi maso awo, zopanga zake 
zazikuluzikulu zimene zisonyeza kuti amene adatha kupanga 
zimenezo sangalephere kuukitsa akufa.Ndipo patsogolo pake 
surayi ikulamula Mneneri (SAW) kuti akumbutse anthu, 
chifukwa kukumbutsako ndiwo udindo wake waukulu kwa 
anthu. Udindo wake iye ndikukumbutsa kokha, osati 
kukakamiza anthu chikhulupiriro. Koma yemwe adzanyozera 
ndi kukanira atakumbutsidwa, Mulungu adzamlanga pamachimo 
ake ndichilango chachikulu pamene adzabwerere kwa Iye 
akamwalira. Chifukwa onse kobwerera kwawo nkwa Iye basi. 
Ndipo onse adzaweruzidwa ndi Iye. 



Surat Al-Ghashiyah LXXXVIII 



m^m 



q^#i(^jJt<&W- 



'^te^** 9 *' 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kodi yakudzera,(iwe 
Mtumiki) (SAW) Nkhani (ya 
Kiyama) imene idzaphimba Anthu 
ndi zoopsa zake? 

2. Nkhope zina tsiku limenelo, ®%£&^ 9 $t*J> 
Zidzakhalazonyozeka, 1 4 * 

1 Tanthauzo la nkhope apa ndi eni nkhopezo. Amene akunenedwa pamenepa 



Surat 88. Al-Ghashiyah Juzu 30 1355 T * *>» AA a-S»^ h*> 



3. Zogwira ntchito yotopetsa 
Kwambiri, 

4. Zikalowa ku moto wotentha 
Kwambiri, 

5. Zikamwetsedwa pa kasupe 
Wotentha kwabasi. 

6. Sadzakhala ndichakudya 
koma minga, 

7. Yosanenepetsa (thupi) 
ndiponso Yosathetsa njala. 

8. Nkhope zina tsiku limenelo 
Zidzakhala zosangalala. 

9. Zidzakondwera ndi malipiro 
A zochita zake (za padziko 
lapansi), 1 

10. M'minda ya pamwamba 
(Jannat): 

11. Sizikamva m'menemo mawu 
oipa, (Otukwana ndi kulaula), 

12. Mmenemo muli a kasupe 
oyenda (Mokongola). 2 

13. Mmenemo muli mabedi a 
pamwamba, 



S'.»«ri> 






h 9 fi 9 9.19 * < S ? 9 h$ 



<^L»V^-ouJ, 






©^ "-'^ 






ndi anthu oipa. Mulungu watchula nkhope chifukwa ndi chiwalo cholemekezeka 
pa chilengedwe cha munthu ndipo ndi pamene pali chithunzi chake. 

1 Tanthauzo la "kukondweretsedwa ndi zochita zawo" ndikuti anthu abwino 
adzakondwera ndi ntchito zawo zabwino zomwe adazichita pa dziko lapansi 
akadzakhala ndi malipiro abwino pa tsiku lomaliza. 

2 (Ndime 12-16) Zosangalatsa zentzeni za tsiku lomaliza monga momwe 
adatiuzira Mneneri (SAW) kuti ku Jannah kuli zinthu zimene diso 
silidapenyepo ngakhale khutu silidamvepo ndipo sizidapitepo m'maganizo a 
munthu. Choncho zokondweretsa izi zimene Mulungu watiuza apa 
akungofanizira ndi zinthu zomwe tikuzidziwa. 



Surat 88. Al-Ghashiyah Juzu 30 1356 T ♦ >>» 



A A ibUll 5jj-» 






© 



14. Ndi zikho zoikidwa bwino 
(Pamaso pawo), 

15. Ndi misamiro yoikidwa 
bwino M'mizeremizere 

16. Ndi mphasa (zamtengo 
wapatali, Carpet) zoyalidwa 
ponseponse. 

17. (Kodi akunyozera 
kulingalira Zisonyezo za 
Mulungu), Sakulingalira 
kungamira idalengedwa Motani? 1 

18. Ndi thambo (limene 
akuliona Nthawi zonse) m'mene 
lidatukulidwira (Kutali popanda 
mzati)? 

19. Ndi mapiri momwe 
adakhazikitsidwira (Molimba)? 

20. Ndi nthaka momwe 
idayalidwira 

21. Basi, kumbutsa (anthu) 
ndithu, Iwe, ndiwe Mkumbutsi. 

22. Sindiwe wokakamiza anthu 
(kuti Akhulupirire 
ndikuwapondereza); 2 

1 (Ndime 17-20)Mulungu akuwauza kuti ayang'ane chilengedwe cha ngamira, 
thambo, mapiri ndi nthaka. Pambuyo pake alingalire, aone kuti amene 
adalenga zimenezo ngotha kuchita chilichonse monga kuukitsa anthu 
m'manda. Cholinga cha Mulungu potchula zinthu zimenezi, ngakhale kuti 
malangizowa nga munthu aliyense, koma adali kuwauza akafiri a pa Makka 
amene zinthu zimenezi maso awo ankaziona nthawi ndi nthawi. 

2 Ayah iyi ikukwana kuwatsutsa adani a Chisilamu amene akunena kuti, 
"chipembedzo cha Chisilamu chidafala ndi lupanga." Kutanthauza kuti 
ankawakakamiza anthu kuti achivomere chipembedzochi. Sichodabwitsa 
kuona adani a Chisilamu akuchinyoza chipembedzochi, koma chodabwitsa 



±>%s,99' * 1///; 

§s#3?&aiais 









Surat 88. Al-Ghashiyah Juzu 30 1357 r * *>i 



A A 4~ittJt *jj~4 



23. Koma amene anyoza ndi 
kukanira (Ulaliki wako), 

24. Mulungu amulanga 
chilango Chachikulu. 

25. Ndithu, kobwerera kwawo 
ndi Kwa Ife basi; 

26. Ndipo ndithu, 
kuwerengedwa Kwawo kuli kwa Ife. 






nchakuti mawu onamawa nkumatulukanso mkamwa mwa anthu omwe 
amadzitcha kuti ndi Asilamu. Nzoona alipo ena mwa anthu odziwa za 
chipembedzo (ma Ulama) amene adanena kuti chipembedzo cha Chisilamu 
chidatetezedwa ndi lupanga.koma simonga momwe akutanthauzirira adani 
amene sadziwa za Chisilamu nkumangotsatira mabodza akuluakulu awo. 
Cholinga cha ma Ulama ponena kuti "Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga" 
kumeneko ndi kudziteteza kwa adani omwe adafuna kuchithetsa, osati 
kuwakakamiza anthu kulowa mchipembedzo. Kukakamiza anthu kulowa 
mChisilamu nkosaloledwa. Amene akudziwa mbiri ya Chisilamu ngakhale 
pang'ono, akudziwa kuti Asitamu sadalamulidwe kuchita Jihad mpaka 
pamene akafiri adafi kuwazunza. Pali nkhani zambiri za Maswahaba (otsatira 
Mneneri) (SAW) ku Madina pamene adafuna kuwakakamiza ana awo kulowa 
m'Chisilamu, koma Mneneri adawakaniza kutero. Basi, munthu amene 
akunena zoterezo mwina akutero pa chifukwa chosadziwa za chipembedzo 
cha Chisilamu, mwinanso nkukhala misala basi. 



Surat 89. Al-Fajr Juzu 30 1358 



*>' 



A^ yjiiJl Qjj~i 




Surayi yayamba ndi kulumbira komwe kwasonyeza zolinga 
zosiyanasiyana zomwe zitembenula maso kuti aone mphamvu 
za Mulungu pa zimenezi potsimikiza kuti amene akukana 
Mulungu ndikutsutsa za kuuka, adzalangidwa monga momwe 
adalangidwira omwe adatsutsa kale. Ndiponso surayi 
ikufotokoza machitidwe a Mulungu poyesa anthu Ake ndi 
zabwino ndiponso zoipa. Ndikuti kupereka Kwake ndi kumana 
Kwake sikusonyeza chikondi Chake ndi nkwiyo Wake. Ndipo 
surayi ikunenetsa za msulizo ndi umbombo womwe anthu ena 
ali nawo. Kenako ikumalizira ndi kulozera za anthu osalabadira 
kuchita zabwino kuti adzalakalaka akadatsogoza zochita 
zabwino kuti zikawapulumutse ataona zoopsa kwambiri za 
tsiku la Kiyama. Ndikuti kudzakhala kuusangalatsa mtima 
wabwino wolungama umene udatsogoza ntchito zabwino, 
powuitanira kukalowa ku Jannah ya Mulungu pamodzi ndi 
anthu abwino. 



Surat Al-Fajr LXXXIX 





^ IMW^ \[ 





M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira kuyera kwa 
M'bandakucha; (pamene usiku 
Uthawa), 

2. Ndi masiku khumi (a Mwezi 
wa Dhul-Hijja omwe ngopatulika 
kwa Mulungu), 1 



o^t^l^W- 



-£> 



sm 






Tanthauzo la aya iyi ndi masiku khumi oiemekezeka omwe ali mkhumi 
loyamba la mwezi wa Dhul-Hijja umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya 
Chisilamu. Amenewa ndi masiku oiemekezeka kuposa masiku onse ngakhale 
masiku a Ramadhan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi 



Surat 89. Al-Fajr Juzu 30 1359 T • *>» 



A^ j*l&\ ojy 



3. Ndi Shaf i ndi Witri: (nambala 
Yogawika ndi yosagawika), 1 

4. Ndi usiku pamene ukupita 
(Chifukwa cha kuyenda kwa dziko 
Kodabwitsa). 

5. Kodi m'zimene zatchulidwazi 
Simuli kulumbira kokwanira, Kwa 
munthu wa nzeru? 

6. Kodi sudadziwe momwe 
Mbuye wako Adawalangira Adi 
(anthu A Mneneri Hud). 

7. Aku Irama; ataliatali ngati 
Zipilala. 2 

8. Omwe onga iwo 
sadalengedwe M'maiko ena? 

9. Ndi Asamudu, (anthu A 
Mneneri Swaleh) amene adali 
Kudula matanthwe ku chigwa 
(Chotchedwa Wadi Qura ndi 
kumamanga Nyumba 
zikuluzikulu)? 

10. Komanso Firiauna (Farawo) 
Mwini magulu ankhondo (omwe 
Amalimbikitsa ufumu wake monga 
Momwe zichiri zimalimbikitsira 
Tenti), 






%$\#^\&&&%i>j 



e$j$\(S2&& 



omaiiza a mwezi wa Ramadhan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa 
mapemphero m'masiku amenewa. 

1 Shaf i ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala 
yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Mulungu pamenepa ndi 
kuzilumbirira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri. 

2 (Ndime 7-9) Adi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu 
matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti, "Ndani wamphamvu 
kuposa ife!" Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali 
kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia. 



Surat 89. Al-Fajr Juzu 30 1360 T * *>» 



A^ >*iJi $jj~* 



11. Amene adaipitsa m'maiko 
mopyola Malire? 

12. Ndipo adachulukitsa 
m'menemo Kuononga (pamwamba 
pakuononga). 1 

13. Choncho Mbuye wako 
adawathira Ndi mitundu ya zilango 
(zoopsa) 

14. Ndithu, Mbuye wako ali 
tcheru (ndi Zochita za anthu. 
Ndipo Akuwasungira kuti 
adzawalipire). 2 

15. Pamene munthu Mbuye 
wake akumuyesa (Mayeso) 
ndikumulemekeza ndi Kumpatsa 
mtendere (wachuma, Ulemerero 
ndi mphamvu) amanena Monyada: 
Mbuye wanga wandilemekeza 
(Chifiikwa zimenezi nzondiyenera 
ine). 

16. Koma akamuyesa mayeso 
ndi kumchepetsera Riziki lake, 
(chuma) amanena (motaya mtima): 
Mbuye Wanga wandinyoza! 

17. Sichoncho ayi, (monga 
momwe mukuganizira) koma inu 
simuchitira za Ufulu ana amasiye! 

18. Ndipo simulimbikitsana za 
Kudyetsa osauka, 















^\&$$&& 



&$&\JX&&1&$1 



©, 



1 Mzinthu zoipa zimene Farawo adachita, ndi kudzitcha kuti iye ndi Mulungu, 
kupha ana achimuna popanda chilungamo, ndi kuwazunza Aisraeli. 

2 Apa ndikuti Mulungu akuwaona anthu Ake nthawi ili yonse. Palibe chimene 
iwo achita popanda lye kuchiona ndi kuchilemba. 



Surat 89. Al-Fajr Juzu 30 1361 T * *>» 



AS j*d\ 5jj- 



19. Ndipo mukudya chuma cha 
masiye; Kudya kosusuka. 1 

20. Ndiponso mukukonda 
chuma; Kukonda kopyola muyeso. 

21. Sichoncho! (Siyani 
machitidwe Amenewa); nthaka 
ikadzapondedwa Pondedwa 
(ndikuifafaniza), 

22. Adzabwera Mbuye wako 
(mmabweredwe Omwe 
akuwadziwa iye mwini) Ndipo 
angero ali mmizere 
Yondondozana. 

23. Basi tsiku limenelo 
idzabweretsedwa Jahannamu, pa 
tsiku limenelo Munthu 
adzakumbukira, koma kukumbuka 
Kumeneko kudzamthandiza 
chiyani? 

24. Adzanena: Kalanga ine! 
Ndikadatsogoza zabwino pa Za 
moyo wangauno! 

25. Motero patsikuli, palibe 
wina Amene adzalange monga 
momwe (Mulungu) adzalangire. 3 

26. Ndiponso sanganjate 
aliyense Monga kunjata kwa iye 
(Mulungu). 

1 Arabu asadalowe m'Chisilamu akazi sadali kugawiridwa chuma cha masiye 
kudzanso ana aang'onoang'ono a masiye sadali kuchiona chumacho 

2 Tanthauzo la "kubweretsedwa Jahanamu" ndiko kuisonyeza kwa anthu. 

3 (Ndime 25-26) Tanthauzo lake ndikuti palibe chofanizira chilango cha 
Mulungu chomwe chidzaperekedwe kwa akafiri ndiponso ndi kunjata komwe 
akafiri adzanjatidwe. 












Surat 89. Al-Fajr Juzu 30 



1362 



r* *>i 



A^ j*iJl 5jj-*» 



27. Ee! Iwe mzimu 
wokhazikika (ndi Choona)! 1 

28. Bwerera kwa Mbuye Wako 
uli wokondwera(ndi zomwe 
Wapatsidwa), ndipo uli 
woyanjidwa (Ndi Mulungu pa 
zomwe udatsogoza). 2 

29. Lowa mgulu la akapolo 
anga abwino, 

30. Ndipo lowa m'munda 
wanga (mnyumba ya Mtendere wa 
muyaya). 



Sfc£]tflJ3SlRg3S 






e^&m 



L, 4 '_,&>£ 




SURAT AL-BALAD XC 




Mulungu walumbirira mzinda wopatulika wa Makka, kwawo 
kwa Mtumiki (SAW) kumene adakulira ndiponso walumbirira 
wobereka ndi woberekedwa. Kudzera mwa iwo udasungidwa 
mtundu wa anthu, kuti ndithu, munthu adalengedwa mmavuto. 
Kenaka Mulungu wafotokoza kuti munthu ali wonyengedwa 
pomaganizira kuti palibe amene angamchite kanthu ndikuti iye 
ngwachuma chambiri. Ndipo kenako Mulungu watchula zina 
mwa zomwe wamdalitsa nazo monga,kumfewetsera njira kuti 
akakhale mmodzi wa anthu a ku Jannah, anthu a kumanja. 



1 "Mzimu wokhazikika" ndi mzimu wa munthu wokhulupirira amene akuchita 
zomwe walamulidwa ndi kusiya zimene waletsedwa. Umenewo ndiwo mzimu 
umene udzakhale wodekha pa tsiku lomaliza chifukwa chakuti pa tsikulo 
sudzakhala ndi mantha kapena kudandaula. 

2 Tanthauzo lake nkuti mzimu wokhazikika udzakondwera ndi zimene 
udzalandira kwa Mulungu tsiku limenelo ndipo naye Mulungu adzakondwera 
nawo. 



Surat 90. Al-Balad Juzu 30 



1363 



r. *>-i 



^ • jULJi hjy~> 



Surat Al-Balad XC 



mm 



Qfa&\<&$Wj 






©oJi^lvjJtj 



®£$&w&& 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira mzinda uwu 
(Wa Makka), 

2. Ndipo iwe udzatsikira mu 
Mdzindawu mwa ufulu (ndi 
Kuuonjezera ulemelero). 

3. Ndiponso ndikulumbirira 
Chobereka ndi choberekedwa, 
(Kudzera mwa iwo mtundu wa 
Anthu udasungidwa); 

4. Ndithudi tamulenga munthu 
mmavuto (Kuyambira chiyambi 
chake Mpaka malekezero a moyo 
wake). 1 

5. Kodi (munthu wolengedwa 
ndi Mavutoyu) akuganiza kuti 
palibe Amene angamuthe? 

6. Akunena (monyadira kuti): 
"Ndaononga chuma chambiri 
(Chifukwa choletsa Chisilamu 
kufala)." 3 



Munthu ali ndi mavuto ambiri amene nyama zina zilibe: chakudya 
amachipeza movutikira, ndipo kudya kwa iye nkofunikira pa moyo wake, 
chovala amachipeza movutikira pomwe iye ndiwoyenera kuvala. Sangathe 
kupirira ndi kutentha kapena kuzizira. Sangathenso kudziteteza popanda 
chida. Ndipo pamwamba pa izi, Ambuye Mulungu amukakamiza zinthu 
zambiri ndi kumuletsanso zinthu zambiri. Ndipo chilichonse chimene iye 
achita chikulembedwa. Pa tsiku lomaliza adzawerengedwa chilichonse 
chimene adachichita; chachikulu kapena chaching'ono. 

2 Tanthauzo lake apa nkuti munthu akuganiza kuti palibe aliyense amene 
angamuweruze pa zolakwa zake. 

3 (Ndime 6-7) Mawu awa akunenedwa kwa okanira omwe adali kupereka 






Surat 90. Al-Balad Juzu 30 



1364 



►>' 



^ * jJLJl 5jj-» 



7. Kodi akuganiza kuti palibe 
Akumuona?. 

8. Kodi sitidampangire maso 
Awiri (amene akuyang'anira)? 

9. Ndilirime ndi milomo iwiri 
(Zimene akulankhulira)? 

10. Ndipo tamlongosolera njira 
ziwiri: (Yabwino ndi yoipa, ndipo 
Tampatsa mphamvu yosankhira 
Njira imene akufuna). 

11. Kodi walikwera phiri lovutalo 
(lomwe lingakamfikitse ku Jannah)? 1 

12. Nanga nchiyani 
chakudziwitsa za Kukwera phiri 
lovutalo? 

13. (Kutero ndiko) kupereka 
ufulu kwa Kapolo, 

14. Kapena kuwadyetsa 
(osowa) pa Masiku a njala, 

15. Amasiye achibale (ndi 
amene Sali achibale), 

16. Kapena wosauka wa fumbi 
Lokhalokha (chifukwa cha 
kuvutika Kwambiri), 






chuma chawo pomenyana ndi Usilamu kapena kufuna kumupha Mneneri 
(SAW). Kenako adali kudzitama chifukwa chopereka chuma chambiri pa njirayo. 
Izi zikumukhudza aliyense amene akufuna kuti Chisilamu chionongeke. 
Ndipo iwo amaganiza kuti Mulungu sakudziwa za maganizo awo oipa. 
1 Tanthauzo lake ndikuti bwanji munthu sathokoza chifundo chimenechi 
(chopatsidwa maso ndi pakamwa) pogwiritsa ntchito chuma chake pa zinthu 
zabwino zimene Mulungu wazitchula m'ma aya akubwerawa? Ndipo 
tanthauzo la "kukwera phiri lovuta" ndiko kupereka chuma panjira ya Mulungu 
chimene chili ndinthu chovuta kwa anthu ambiri ndipo chimafanana 
ndikukwera phiri losongoka . 



Surat 90. Al-Balad Juzu 30 



1365 



r% *j*-i 



^ • jJUl Sjj-- 



17. Komanso nakhala mmodzi 
Mwa okhulupirira 
ndikumalangizana Za 
kupirira,ndiponso za chifundo. 

18. Otero ndiwo (anthu abwino) 
A ku dzanja lamanja. 

19. Koma amene 
sanakhulupirire aya Zathu, ndi 
anthu a kudzanja Lamanzere 
(oipa). 

20. Moto wozungulira mbali 
zonse Udzakhala pa iwo 
(ndikuwatsekera Makomo). 







SURAT ASH-SHAMS XCI 




Mulungu walumbirira zinthu zambiri mzolengedwa Zake 
zazikuluzikulu koyambirira kwa surah iyi zomwe zikusonyeza 
kukwanira kwa mphamvu Zake ndi umodzi Wake potsimikiza 
kuti wapambana amene wayeretsa mtima wake ndi 
chikhulupiriro chake ku uchimo ndi kumvera Mulungu. 
Ndiponso kuti wataika amene waudetsa ndi machimo ndi 
kukanira Mulungu. Kenako surayi yafotokoza nkhani ya 
Asamud omwe adali anthu a Swaleh ndi zimene zidawatsikira 
kuti aliyense wa makani ndi wotsutsa aphunzire kupyolera mwa 
iwo. 

Iwo pamene adamkanira Mneneri wawo ndikupha ngamira 
yoletsedwa, Mulungu adawaononga onse.Iye Mulungu saopa 
kanthu pazotsatira zakuwaononga kwawo, chifukwa lye 
safunsidwa zimene akuchita. Adawatsitsira chilango 
choyenerana ndi makhalidwe awo oipa. 



Surat 91. Ash-Shams Juzu 30 1366 ? • *>» 



^ ) ^w Jl 3jJ-J 



Surat Ash-Shams XCI 



■**■ 



g^US^ 



o^l^jll^U- 



-£> 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira dzuwa ndi 
Dangalira lake, 

2. Ndi mwezi pamene 
ukulitsatira (dzuwalo Ndikulowa 
mmalo mwake powalitsa Litalowa), 

3. Ndi usana pamene ukulisonyeza 
Poyera (kuti lisaphimbidwe), 

4. Ndi usiku pamene ukuliphimba, 

5. Ndi thambo ndi (Mwini 
mphamvu ZonseWamkulu) yemwe 
adalimanga Ndikulitukula 
(mwaluso), 

6. Ndi nthaka ndi(Mwini 
mphamvu zonse Wamkulu), 
yemwe adaiyala (mbali Zonse 
ndikuchita kukhala ngati Choyala), 

7. Ndimzimu ndi yemwe 
adawulinganiza (poupatsa 
mphamvu); 

8. Ndipo adaudziwitsa zoipa zake 
ndi Zabwino zake: (ndikuupatsa 
ufulu Ndi mphamvu zochitira 
zimene Ukufiina). 

9. Ndithu, wapambana amene 
wauyeretsa. 1 

1 Kuyeretsa mzimu ndiko kuukongoletsa ndi maphunziro ndi ntchito zabwino. 
Zimenezi ndizo zimamkwanitsa munthu kuti atchulidwe munthu. Ndipo zimenezi 
ndizo zingapereke ulemerero kwa munthu pa dziko mpaka pa tsiku lomaliza. 



<^c^(j^-£l!S 



£>14*& %&™3 



\£^^t&3\j 



©t^Uj^S'b 












Surat 91. Ash-Shams Juzu 30 



1367 



.jA-i 



^ ) j^gJtJl 5jj-*» 



"ite^lU 



^i&^i&SjtfJOSi 



©I 



*fl-**J 



10. Ndipo ndithu,wataika 
amene Wauononga. 1 

11. Thamud (Samudu) adakanira 
(Mneneri wawo) chifukwa cha 
Kulumpha malire kwawo. 2 

12. Pamene woipitsitsa wawo 
Adadzipereka (kupha ngamira 
Yozizwitsa). 

13. Pamenepo Mneneri wa 
Mulungu (Swaleh) adawauza: 
"Isiyeni ngamira ya Mulungu (Idye 
mdziko la Mulungu). Musailetse 
kumwa madzi (pa Tsiku lake). 

14. Koma adamutsutsa ndikuipha; 
kwa Chifukwa chimenecho Mbuye 
wawo (Mulungu) adawaononga 
chifukwa Cha tchimo lawo; 
adangowafafaniza (Onse mnthaka). 

15. lye saopa zotsatira za 
chilangochi (Chifukwa amenewa 
ndi malipiro A chilungamo pa 
zomwe adachita). 



Kuwuononga mzimu ndiko kuuchitira mphwayi; kungoulekerera 
ndikumautsatira pa zimene ufuna mpaka kulowa mu uve ndi m'machimo a 
umbuli ndipo ndi kuonongeka pa dziko lino mpaka Pa tsiku lomaliza. 
2 (Ndime 11-15) Asamudu atchulidwa m'surat AL-FAJR. Anthu awa 
adamukana Mtumiki wawo, Mtumiki Swaleh (AS); adamuuza kuti ngati afuna 
amukhulupirire, atulutse ngamira kuchokera mthanthwe, apo ndipo 
adzamukhulupirira kuti ndi Mneneri. Swaleh adampempha Mulungu, ndipo 
lidasweka thanthwe lija ndikutulukamo ngamira monga momwe adafunira 
anthu aja. Koma sadamukhulupirirebe. 

Mneneri Swaleh (AS) adawauza kuti:"Chenjerani ndi ngamira ya Mulungu iyi, 
musaikhudze ndi choipa chilichonse." Ndipo adawakakamiza kuti pa tsiku 
limene ngamira ija ikumwa madzi, iwo asatunge madzi. Ndiponso pa tsiku 
limene iwo akutunga madzi.ngamira siidzamwa madzi. Koma adamkanira. 
Ndipo m'modzi wa iwo amene adali wamphulupulu adaipha ngamira ija. 
Mulungu nthawi yomweyo adawatsitsira chilango chifukwa cha machimo awo, 
chomwe chidawakwanira onse kuyambira uja wopha ngamira ndi ena onse. 









® <jt^<J>Qyj 



Surat 92. Al-Lail 



Juzu 30 



1368 



,>i 



*Y JJUlJjj- 




Mulungu wolemekezeka akulumbirira zinthu zitatu msurah 
iyi, potsimikiza kuti ntchito za anthu nzosiyana: zina 
nzolungama pomwe zina nzosalungama. Ndikuti amene 
akupereka za ulele, ndi kuopa Mulungu ndikuikira umboni 
mwachilungamo pazinthu zabwino, Mulungu amfewetsera njira 
zabwino. Ndipo amene wachita umbombo ndikuziganizira kuti 
ngoima payekha ndikumatsutsa mawu abwino, Mulungu 
amfewetsera njira zopita kumavuto. Ndipo chuma chake 
sichidzamthandiza kumchotsa mmavuto, akadzafa. 

Ndipo kenaka surayi ikufotokoza kuti Mulungu ndiye mwini 
udindo wolongosolera anthu njira ya chiongoko. Ndikuti moyo 
watsiku lomaliza ndi moyo wadziko lapansi ngwake. Ndiponso 
yachenjeza za chilango cha moto chomwe anthu oipa 
akalangidwa nacho pomwe abwino akapulumuka. 



Surat Al-Lail XCII 



oi^lt^ll^ 



-^ 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira usiku 
pamene Ukuphimba (chilichonse), 

2. Ndi usana pamene kukuyera, 

3. Ndiponso Yemwe adalenga 
Chachimuna ndi chachikazi, 

4. Ndithu, zochita zanu 
nzosiyanasiyana. l 

1 Tanthauzo lake ndikuti mwa anthu alipo ena amene amachita zabwino ndipo 
ena amachita zoipa. Ena amagwira ntchito zothandiza pambuyo pa imfa pamodzi 
ndi kutumikira Mulungu. Ndipo pali ena omwe amangokhala otanganidwa ndi 
zadziko lapansi. Ena amachita zinthu zopindula pomwe ena satero. 



W;;#ji#a: 



•• 



<2V&^"- 



0\ 



Siirat 92. Al-Lail 



Juzu 30 



1369 



r* *>t 



S Y JJLi* 5jj- 



5. Tsono yemwe akupereka (pa 
njira Ya Mulungu) ndikumamuopa 
(Mbuye Wake ndikupewa 
zoletsedwa), 1 

6. Ndikumavomereza zinthu 
zabwino; (Komwe kuli 
kukhulupirira Mulungu 
Mwanzeru), 2 

7. Timufewetsera njira 
yompititsa ku zabwino. 3 

8. Koma uyo achite umbombo 
ndikuganiza Za kuti iye payekha 
ngokwana; 

9. Ndi kumatsutsa zinthu 
zabwino, 

10. Timufewetsera njira 
yompititsa Ku mavuto (a muyaya). 

11. Chumachake 
sichidzamthandiza (Chilichonse) 
akadzagwera ku moto. 

12. Ndithu, Ife ndi amene 
timawalongosolera Anthu njira 
yabwino ndi njira yoipa. 

13. Ndipo ndithu, moyo 
womaliza ndi Moyo woyamba uli 
m'manja mwathu. 



ajsijcWSfc 






A ) 9 9 9 \ l 9v'9"< 



1 Tanthauzo lake apa ndikupereka chuma ndi kudzipereka pa zauzimu. Ndiye 
kuti munthu agwiritsire ntchito chuma chake m'njira ya Mulungu ndiponso kwa 
anthu anzake. Ayeneranso kudzipereka iye mwini pa moyo wauzimu. 

2 Tanthauzo la "Kuvomereza zinthu zabwino" ndiko kugwirizana nazo zimene 
Mulungu walamula, chifukwa chakuti lye amalamula zinthu zabwino 
zokhazokha ndikuletsa zoipa. 

3 Tanthauzo la aya imeneyi ndikuti: Timufewetsera njira yochitira zinthu 
zabwino mpaka kufikira kuti akapanda kuchita chinthu chabwino sapeza 
mtendere mumtima mwake. 



Surat 92. Al-Lail Juzu 30 1370 T * *>» 



M JJJio^ 



14. Basi, ndikukuchenjezani za 
Moto woyaka mwa mphamvu; 

15. Palibe amene akaulowe 
Koma (Kafiri) woipitsitsa 
kwambiri, 

16. Yemwe amakanira (choona) 
ndi Kunyoza (zisonyezo za 
Mulungu). 

17. Koma yemwe akuopa 
Mulungu Kwambiri 
akatalikitsidwa ndi moto; 

18. Amene akupereka chuma 
chake Ndi cholinga chodziyeretsa. 

19. Ndipo palibe aliyense Kwa 
iye, amene adamchitira za 
Chifundo zomwe zikulipidwa. 1 

20. Koma ( akuchita zimenezi) 
Kufuna chikondi cha Mbuye wake 
Wa pamwambamwamba. 

21. Ndipo posachedwa 
adzasangalala. 2 






® Jyi'v^^l 



WKg^i 



S (SU^oM(i^ 






h&$\$>&ft£ 






1 (Ndime 19-20)Tanthauzo la ma aya awiri awa nkuti munthu uyu sakupereka 
chuma chake chifukwa chobwezera chifundo cha anthu, kapena kuti 
adzamubwezerenso iye chifundo, koma akupereka chifukwa chofuna chikondi 
cha Mbuye wake basi. 

2 Tanthauzo lake apa ndikuti Mulungu adzamukondweretsa ndi malipiro Ake 
abwino kufikira munthuyo adzakondwera. Ma aya, kuyambira 17 mpaka 21, 
adatsika chifukwa cha Sayyidina Abu Bakr (RA) yemwe adali kupereka chuma 
chake powagula akapolo omwe adali kuzunzidwa ndi mabwana awo chifukwa 
cholowa Chisilamu, pambuyo pake amawapatsa ufulu. Ndipo m'modzi wa 
iwowa ndi Sayyidina Bilal amene adali Muazzini wa Mneneri Muhammad 
(SAW). Chomwechonso aya zimenezi zikumkhudza aliyense amene 
akugwiritsa ntchito chuma chake mnjira yopulumutsira chipembedzo. 



Surat 93. Adh-Dhuha Juzu 30 



1371 



T * frj£-t \T ^-iait $j>-> 




Surayi yayamba ndi kulumbira kuwiri kulumbirira nthawi 
yogwiridwa ntchito ndi nthawi yopumula, potsimikiza kuti 
ndithu, Mulungu sadasiye Mneneri Wake kapena kumuda. 
Ndipo zimene wamkonzera tsiku lomaliza ndizabwino kuposa 
zimene wamdalitsa nazo padziko lapansi. Kenaka Mulungu 
walumbira kuti adzampatsa kufikira atakondwera monga 
momwe adampezera ali wamasiye ndipo adamsunga; ali 
wosazindikira Qur'an ndipo adamuongola bwino 
pomuzindikiritsa Qur'aniyo; ali wosauka ndipo adamlemeretsa. 

Kenako surayi ikulimbikitsa zochitira chifundo amasiye 
ndikuletsa kukalipira opempha ndikutinso tikhale tikunena za 
Mtendere wa Mulungu umene uli paife posonyeza kuthokoza. 



Surat Adh-Dhuha XCIII 



ti^l££ _ '#' 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira masana 
dzuwa Litakwera (imene ili nthawi 
Yantchito), 

2. Ndi usiku pamene 
ukuvindikira, 

3. Sadakusiye Mbuye wako 
(iwe Mneneri) (SAW) ndiponso 
sadakude. 1 



o^t^i^U- 



"Wwb 









1 M'masiku oyamba pa chiyambi cha Usilamu, padapita masiku angapo 
Mtumiki (SAW) osamutsikira chivumbulutso. lye poona izi adali kukaika ndi 
kudandaula kwakukulu, nao okanira apa Makka adali kumchita chipongwe. 
Adali kumunena kuti, "kodi Mbuye wako wakusiya kapena wakukwiira?" Basi 
apa Mulungu akumutonthoza Mneneri Wake, pamodzi ndi kuwayankha 
okanira aja kuti, "Sadamusiye ndipo sadakwiye naye." 



Surat 93. Adh-Dhuha Juzu 30 



1372 



r» s-jjfc-i sr ti5 iwjiii 5jj-- 



4. Ndithu, umoyo watsiku liri 
Mkudza ndi wabwino kwa iwe 
Kuposa umoyo woyambawu. 1 

5. Ndithu posachedwapa 
akupatsa Mbuye wako (zabwino 
zamdziko Lapansi ndi tsiku 
lomaliza) Ndipo ukondwera. 2 

6. Kodi sadakupeze uli wa masiye 
Ndipo adakupatsa pokhala pabwino? 

7. Ndipo adakupeza uli 
wosazindikira (Qur'an) 
Nakuongola (pokuzindikiritsa 
Qur'aniyo ndi Malamulo a 
chipembedzo)? 3 

8. Ndiponso adakupeza uli 
Wosauka Nakulemeretsa? 

9. Basi, wamasiye usamchitire 
nkhanza.. 

10. Ndiponso wopempha 
usamukalipire. 

11. Tsono mtendere wa Mbuye 
wako Uwutchule (pothokoza ndi 
Kugwira ntchito zabwino). 






* i -VV A *Fl 






1 Ayah iyi ikulozera kuti tsiku lililonse lomwe likubwera zochita za Mneneri 
zidzankerankera patsogolo. Mmenemo ndimomwe zidalili chipembedzo 
chimatukuka kupita patsogolo. Ndipo 

2 Zopatsidwa zomwe adalonjezedwa apa ndi Mulungu wake, ndi zapadziko 
mpaka kumwamba (Akhera). Padziko lapansi adampatsa chilichonse chimene 
adali kuchilakalaka monga kuwaongola anthu ake, kuchilemekeza chipembedzo 
chake ndi kuwagonjetsa adani ake. Zonsezi Mulungu adamchitira mnyengo 
yochepa modabwitsa. 

3 Mneneri Muhammad (SAW) asanapatsidwe uneneri wake ndi Mulungu anali 
kudandaula kwambiri poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye 
sadali kudziwa momwe angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku 
mapiri amene adali pafupi ndi mzinda wa Makka. Kumeneko adali kupemphera 
ndi kumalingalira ndi kupempha Mulungu kuti amusonyeze njira yachiongoko. 



Surat 94. Ash-Sharh Juzu 30 



1373 



.j* 



H i Cr tJl ijj* 



J^ SURAT ASH-SHARH XCIV 

r Lrc^zzrLKrY .w-rv^ _— _ . 





Surayi ikulongosola kuti Mulungu adaphanula chifuwa cha 
Mneneri (SAW) ndikuchichita kukhala potsikira zobisika ndi 
maphunziro. Ndipo adamchotsera zomwe zinkalemeretsa msana 
wake pantchito yolalikira. Ndipo Mulungu analumikiza dzina 
Lake ndi iye pa mawu amaziko a chikhulupiriro ndi mzinthu 
zina zazikuluzikulu mchipembedzo. Kenako surayi yalongosola 
za machitidwe a Mulungu pophatikiza zabwino ndi zovuta, 
ndipo Mtumiki akuuzidwa kuti akachita chabwino, 
achitsatizenso ndi chabwino china; ndikuti cholinga chake pa 
zonse chikhale kwa Mulungu. Iye ndiwakutha kumthandiza. 



Surat Ash-Sharh XCIV 



M' dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kodi sitidachiphanule 
chifuwa Chako (pokupatsa 
chiongoko ndi Chikhulupiriro ndi 
nzeru zambiri)? 1 

2. Ndipo takuchotsera mtolo 
Wako (pantchito yolalikira 
pokuthandiza Ndi kukufewetsera 
zinthu zako); 

3. Mtolo umene udalemetsa 
msana Wako? 

4. Ndipo takukweza 
kutchulidwa kwako. 2 



o^ly^jM^U- 



-2> 



OiljOud^I^i^J I 






h2^(j^\($o$\ 



W)^z& 



1 Kuchiphanula chifuwa, kumeneko ndiko kuchotsa chikaiko choipa. 

2 Mulungu wakukweza kutchulidwa kwa Mtumiki Muhammad (SAW) 
pakumpatsa uneneri kumchitira zabwino kuposa aneneri ena, kuchipanga 
chipembedzo chake kukhala chotsiriza chosafafanizidwa ndi Mtumiki wina. 



Surat 94. Ash-Sharh Juzu 30 I 1374 T • *>» 



^ £ £j-*Jl 5jj-» 



5. Ndipo ndithu, pali chovuta 
palinso zabwino (Zambiri). 

6. Ndithu pali chovuta palinso 
zabwino (zambiri). 

7. Basi, ukamaliza ntchito 
(yolalikira Ndi Jihad) limbikira 
kupemphera. 1 

8. Ndipo khala wolakalaka 
(zabwino zomwe zili) Kwa Mbuye 
wako. 







M'surayi Mulungu akulumbirira zipatso ziwiri zodala, ndi 
malo awiri abwino potsimikiza kuti lye adalenga munthu 
mkalengedwe kabwino: pompatsa nzeru ndikukhala ndi ufulu 
pa zofuna zake. Kenaka surayi yalongosolanso kuti munthu 
sadachite motsatiza chilengedwe chake ndipo watsika pa 
ulemerero wake ndikukhala wapansi kuposa wapansi, kupatula 
amene akhulupirira ndikumachita zabwino. 

Kenako surayi yadzudzula amene akukanira za kuuka 
mmanda ataona kale zizindikiro zake zosonyeza mphamvu za 
Mulungu ndi luso Lake. 



Ndipo ndi chopambana kuposa zipembedzo zonse zomwe zidatsogola, 
ndiponso ndi chomwe chingawathandize anthu onse osiyana mitundu, pa 
nyengo zonse ndi pamalo pali ponse. 

1 Tanthauzo lake nkuti, "Ukamaliza ntchito yako yolalikira kwa anthu zomwe 
Mulungu wakutuma kuti ulalikire.chita mapemphero ambiri.umthokoze Mbuye 
wako pa chisomo Chake chimene wakudalitsa nacho." Mneneri (SAW) adali 
kulimbikira kwambiri pochita mapempheroMwakuti amaima ndi kumapemphera 
kufikira miyendo yake kutupa. Amagwetsa mphumi pansi (sijida) mpaka 
kuganiziridwa kuti wafa chifukwa cha kutalika kwa nthawi yopempherayo. 



Surat 95. At-Tin 



Juzu30 1375 r» tji-i 



^0 jjl Ojj-** 



Surat At-Tin XCV 



~j^^ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira mitengo ya 
Mkuyu Ndi Zitona (pansi pa 
Mitengo Imeneyi Ibrahim ndi Nuh 
(Nowa) Adapeza uneneri), 

2. Ndi phiri la Sinai (pamene 
Mulungu adamulankhulira Musa), 

3. Ndiponso Mzinda uwu 
(wolemekezeka) Wamtendere: 
(Makka,womwe Adapatsiridwa 
uneneri Muhammad) (SAW), 

4. Palibe chikaiko, tamulenga 
munthu Mkalengedwe kabwino, 
kolingana (Ndipo ali ndi mbiri 
zabwino); 1 

5. Pambuyo pake tamubwezera 
pansi Kumposa wa pansi; 2 

6. Kupatula amene 
akhulupirira Ndikumachita 
zabwino, adzakhala Nawo iwo 
malipiro osatha. 

7. Tsono nchiyani chakuchititsa 
kuti Ukanire kuuka ndi malipiro 



o&g\uP&\&\j 



^%%<$$* 






0(^JtonilJ^j 



®^^^p>!^(yU^lwtoual 






©^OilJ^^^ 



1 M'gulu la nyama palibe yopambana kuposa munthu mkalengedwe ndi pa 
nzeru. 

2 Munthu ali ndi makhalidwe awiri: Ngati agwiritsa ntchito nzeru zake 
amaongoka ndipo amaiposa nyama iti yonse. Koma ngati sagwiritsa ntchito 
nzeru zake amasokera ndi kukhala wapansi kuposa nyama zonse. 



Surat 96. Al-'Alaq Juzu 30 



1376 



*>' 



^1 jUJl ijj-* 



pambuyo (Poona mphamvu zathu 
pachilichonse)? 1 

8. Kodi Mulungu si Muweruzi 
wa nzeru Kuposa aweruzi onse? 



hti^P&\{$ 




SURAT AL- 4 ALAQ XCVI 




M'surayi akutilimbitsa za kuphunzira kuwerenga ndi 
kulemba. Ndikuti amene adatha kumlenga munthu kuchokera 
kuchinthu chofooka angathe kumphunzitsa kulemba kuti 
maphunziro asungidwe ndi kulembako: ndikuti azimvana 
kupyolera mkulembako. Ndiponso ndikumphunzitsa zomwe 
sadali kuzidziwa. 

Surayi ikufotokozanso kuti nthawi zina chuma ndi mphamvu 
zimachititsa mtima wa munthu kupyola malire. 



Surat Al-'Alaq XCVI 



m 



o£*2l<y*f£t>iU- 



-^ 



©^j^^lpl 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Werenga! (Iwe, Mneneri 
(SAW), zomwe 

Zikuvumbulutsidwa) Mdzina la 
Mbuye Wako yemwe adalenga 
(zolengedwa Zonse). 2 



1 (Ndime 7-8) Mulungu akuuza munthu kuti: Pambuyo podziwa kuti Mulungu 
ndi yemwe adapanga zimenezo, ndi chiyani nanga chikumukaikitsa za tsiku la 
chiweruzo? 

2 Tanena kale mndemanga 7 yamu surat - Dhuha kuti Mneneri Muhammad 
(SAW) asadapatsidwe Uneneri wake ndi Mulungu adali kudandaula kwambiri 
poona anthu ake ali osokera ndiponso poona kuti iye sadali kudziwa momwe 
angawaongolere. Pambuyo pake adali kumapita ku mapiri amene adali 
pafupi ndi Mzinda wa Makka.Kumeneko adali kupemphera ndi kumalingalira 



Surat 96. Al-'Alaq Juzu 30 1377 T * fr j*-i 



^ 1 jWl dj^-* 



2. Adalenga munthu kuchokera 
Kumagazi owundana, 1 

3. Werenga! Ndipo Mbuye 
wako ndi Mfulu, 2 

4. Yemwe waphunzitsa 
(munthu Kulemba) ndi 
cholembera. 

5. Waphunzitsa munthu zinthu 
(Zambiri) zomwe (iye) sadali 
Kuzidziwa. 

6. Zoona ndithu, koma munthu 
Akupyola malire (podzikweza Ndi 
Mulungu wake), 

7. Chifukwa chodziona kuti 
walemera. 

8. Palibe chikaiko, (iwe 
Mneneri (SAW) Kobwerera 






ndi kupempha Mulungu kuti amusonyeze njira ya chiongoko. Choncho tsiku 
lina pamene adati ku phanga la Hiraa, pafupi ndi Makka ali mkati 
mopemphera, Mngelo adamuonekera mwadzidzidzi nati: "Iwe Muhammad! 
Ine ndine Jiburil (Gabriel) ndipo iwe ndiwe Mtumiki wa Mulungu kwa 
zolengedwa zonse!" Pambuyo pake adamuuza kuti, "werenga!" Mneneri 
adayankha, "Ine sindidziwa kuwerenga." Jiburil uja adamgwira ndi kumpana 
mwamphamvu mpaka adavutika kwambiri. Adamsiyanso ndi kumuuza, 
"werenga!" Mneneri adayankha monga adamuyankhira poyamba mpaka 
kadakwana katatu akumuchita zokhazokhazo. Kenaka adamuwerengera ma 
ayah kuchokera 1 mpaka 5. Ma ayah amenewa ndiwo oyamba 
kuvumbulutsidwa m'Qur'an. 

1 Madzi ambewu ya munthu, pambuyo pokhazikika mchiberekero kwa masiku 
makumi anayt, amatembenuka ndikukhala magazi. Hi ndiio tanthauzo la ayah 
imeneyi. 

2 Ayah 3 ndi 5 zikukhala ngati kuti Mtumiki (SAW) akuyankhidwa pa kunena 
kwake kwa kuti "Ine sindidziwa kuwerenga." Choncho Mulungu akumuuza kuti 
lye ndi mfulu weniweni, ndi yemwe adawaphunzitsa anthu kulemba ndi 
cholembera ndi zonse zomwe sadali kuzidziwa. Kwa ufulu Wake wochuluka 
ndi mphamvu Zake pa chilichonse, sichovuta kwa lye (Mulungu) 
kumphunzitsa Mtumiki Wake kuwerenga molakatula. 



Siirat 96. Al-'Alaq Juzu 30 137J 


t r* *j*-i ^ jWis^ 


(onse) nkwa Mbuye wako Basi; 
(adzawaukitsa). 1 




9. Kodi wamuona yemwe 
akuletsa, 


teiis 


10. Kapolo (wa Mulungu) 
akamapemphera? 




11. Tandiuza ngati ali 
pachiongoko. 


< ^&\#&v& 


12. Kapena kuti akulamulira 
zoopa Mulungu? 


®^i^ijj 


13. Tandiuza (za woletsayo) 
ngati Akutsutsa (zimene wadza 
nazo Mneneri) ndikunyoza 
(chikhulupiriro Ndi ntchito 
yabwino)? 




14. Kodi sakudziwa kuti 
Mulungu Akuona (machitidwe 
ake.Ndipo Adzamlipira)? 


%»&;©! 


15. Ayi ndithu, ngati sasiya 
Timukoka tsitsi lapaliwombo; 
(Tiligwira mwamphamvu liwombo 
Lake ndikukamponya kumoto). 


^IXfL3ll&$&$& 


16. Liwombo labodza 
(ndiponso) lamachimo. 


fypffiiiX 


17. Basi aliitane gulu lakelo, 
(La amene amakhala nawo 
pabwalo Kuti amthandize pano 
padziko Kapena tsiku lomaliza), 





1 Tanthauzo lake nkuti musanyengedwe ndi chumacho chifukwa chakuti, 
popanda chikaiko, mubwerera kwa Mbuye wanu ndipo chumacho 
sichidzakuthandizanl chilichonse pa maso Pake. 



Surat 97. AI-Qadr Juzu 30 



1379 



r* «.jJrl 



^V jJili Sjj~*> 



18. Nafe tiitana azabaniya 
(angelo aku Moto ). 

19. Ayi ndithu, usamumvere 
(Pa zimene akukuletsazo); Koma 
gwetsa nkhope yako, Pansi ndipo 
dziyandikitse Kwa Mbuye wako. 






&\ 9 Z2i' * 99\' \*\~ v\a& 

2) ^^bu^Jj Aj&2>y*y6 



<3> 




M'sura imeneyi muli kunenedwa za ulemerero wa Qur'an ndi 
za ulemerero wa usiku womwe mkati mwake idavumbulutsidwa. 
Ndikuti usiku umenewo ngwabwino kuposa miyezi chikwi 
chimodzi. Ndikutinso angelo ndi Jiburil amatsika mu usikuwo 
potsatira lamulo la Mbuye wawo pa chinthu chilichonse. Ndipo 
usikuwo umakhala wa mtendere wokhawokha popanda chovuta 
kapena choipa, mpaka kutuluka kwa m'bandakucha. 



Surat Al-QadrXCVII 



&m& 



m 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndithu taivumbulutsa 
(Qur'an) Mu usiku wa Laila - tul - 
Qadr (Usiku wolemekezeka). 1 



oA*><**2L<i>W- 



-z* 



^\M/&i 



1 Qur'an mwachidziwikire idali kuvumbulutsidwa pang'onopang'ono kuchokera 
ku thambo loyamba (Baitul Izza). Choncho, usiku umene idatsika kuchokera ku 
thambo la seveni (Lauh Mahafudwi) kupita ku thambo loyamba udali usiku 
wotchedwa Laila - tul - Qadr (usiku wolemekezeka kwambiri) ndipo ndi chifukwa 
kukunenedwa kuti Qur'an idatsitsidwa mu usiku wa LAILA-TUL-QADR. 
Umenewu ndi usiku umodzi mkati mwa mwezi wa RAMADHANI omwe uli 
wodalitsidwa kuposa miyezi chikwi chimodzi. Tanthauzo lake apa ndikuti munthu 
ngati achita ntchito zabwino mu usiku umenewu amapeza malipiro monga a 
yemwe wachita ntchito zabwino kokwanira miyezi chikwi chimodzi. Ndiponso 
amene achita zoipa mu usiku umenewu amapeza machimo onga yemwe 
wachita zoipa kokwanira miyezi chikwi chimodzi. Koma Mulungu adaubisa 



Surat 97. Al-Qadr Juzu 30 1380 



*>• 



*V jJUtfl Sjj~* 



2. Ndi chiyani chingakudziwitse 
za Usiku wolemekezekawu? 

3. Usiku olemekezekawu uli 
wabwino kuposa Miyezi 1000 
(yomwe Mulibe Laila - tul - Qadr). 

4. Amatsika Angelo ndi Jiburil 
Mmenemo potsatira lamulo la 
Mbuye wawo Mulungu 
kudzalongosola chinthu Chilichonse. 

5. Mtendere!... usiku umenewo, 
(Palibe mavuto ndi zoipa) mpaka 
M'bandakucha. 1 



©j^r^^fs 



&Jfc ^ y $iKhy& I ^jjj 






fe^l^jy^ 



^URATAL-BAYYINAH XCVIII^^Sii 

___ ^__^_ ^ ^^^ ^a^Mj 



„S^: 



Anthu a mabuku adadziwa kupyolera mmabuku mwawo 
mbiri za Mneneri yemwe adzadze kumalekezero a nthawi, 
yemwe ndi Muhammad (SAW). Ndipo nawo Amushirikina a 
m'Madina adadziwa za zimenezi kupyolera mwa eni mabuku 
aja. Choncho chifukwa cha kudziwa kumeneku padafunika 
kumkhulupirira Mneneriyo, akaperekedwa. Koma pamene 
Mneneri wa Mulungu Muhammad (SAW) adaperekedwa kwa 
iwo pamodzi ndi buku la Qur'an, adatsutsana ndipo adaswa 
lonjezo lawo. Choncho zotsatira za kuswa lonjezo lawolo, eni 
mabuku, ndi zoipitsitsa kuposa Amushirikina. Onsewa 
adzakhala ku moto muyaya tsiku lomaliza. Koma Asilamu, eni 



usiku umenewu. Sukudziwika kuti uli pa deti lanji ncholinga choti anthu 
alimbike kuchita mapemphero mwezi wonse wa RAMADHANI; koma 
ukuyembekezedwa kuti uli mu masiku khumi omaliza, makamaka usiku 
woukira pa 21, 23, 25, 27 ndi 29 Kwa yemwe akufuna kupeza madalitso a 
usiku umenewu alimbike kuchita mapemphero kwambiri mwezi wonse. Ndipo 
apa sikuti usikuwo umakhala ndi chizindikiro cha mtundu wina uliwonse 
kusiyana ndi usiku wina, iyayi 

1 Adanena BAIDHAWY kuti tanthauzo la aya iyi ndikuti mu usiku umenewu 
Mulungu amalamula kuti kukhale mtendere wokhawokha. Koma muusiku wina 
amalamula kuti kukhale mtendere ndi masoka. 



Surat 98. Al-Bayyinah Juzu 30 1381 



*>' 



^A 4~Jl OjJ-* 



ulemelero, ndiwo zolengedwa zabwino. Malipiro awo 
ndikukhala muyaya ku Jannah, ku munda wa mtendere, 
ndikukondweretsedwa ndi zimene adzazipeze; zomwe adali 
kuzifuna. Malipiro awo adzawapeza amene adali kuopa Mbuye 
wake. 



Sural Al-Bayyinah XCVIII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Amene adakanira (Mulungu 
ndi Mthenga Wake) mwa omwe 
Adapatsidwa Buku ndi 
Amushirikina Sadali olekana (ndi 
umbuli wawo Ndikusalabadira 
kwawo choona) Mpaka pom we 
chidawadzera chisonyezo 
Choonekera poyera, 1 



#- mw? 



o^l^jll^W- 



-^ 






"Akafiri" omwe adapatsidwa buku, ndi Ayuda ndi Akhristu. "Amushirikina" ndi 
omwe adali kupembedza mafano. Tanthauzo la ma aya awa 1- 4 ndikuti 
asadatulukire Muhammad (SAW), Ayuda ndi Akhristu omwe adali ku Madina, 
pamene adali kuwauza Amushirikina kuti, "Yayandikira nthawi yotulukira 
Mneneri. Ife tidzamtsatira, tidzakhala pamodzi ndi iye. Tidzakumenyani 
nkhondo mpaka kukugonjetsani." Adali kuyembekezera kuti Mneneriyo 
adzakhala mwa iwo. Pamene adali kumva izi, opembedza mafano aja, adali 
odandaula. Iwonso adali kuyembekezera Mneneriyo; limeneli ndilo tanthauzo 
la mawu aja oti: "Sadali olekana mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo 
choonekera poyera". 

Apa ndiye kuti fuko lililonse mwa mafuko atatu aja lidali ndi mtima wopitiriza 
zipembedzo zawo, osaleka mpaka chiwafikire chisonyezo. Tanthauzo la 
"chisonyezo," apa ndi Muhammad (SAW) monga aya yachiwiri yafotokozera. 
Pamene adafika Mneneri, opembedza mafano aja ndiwo adayamba 
kumukhulupirira, koma Ayuda ndi Akhristu pamene adaona kuti Mneneri sali 
wochokera mwa iwo monga m'mene adali kuyembekezera adakhumudwa; 
ena mwa iwo adamkhulupirira pomwe ena sadamkhulupirire. Hi ndilo 
tanthauzo lakuti, "sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe 
chidawafikira chisonyezo." 



Surat 98. Al-Bayyinah Juzu 30 



1382 



*>' 



<\A 



I 0jJ~> 



2. (Yemwe ndi) Mneneri 
wochokera Kwa Mulungu 
akuwawerengera Makalata 
oyeretsedwa (ku zonama). 1 

3. Omwe mkati mwake muli 
malamulo Oongoka (ofotokoza za 
choona). 2 

4. Sadalekane omwe 
adapatsidwa Mabuku mpaka 
pomwe chidawafikira Chisonyezo 
(chosonyeza kuti Muhammad 
(SAW) ndi mthenga wa Mulungu 
Yemwe adalonjezedwa mmabuku 
awo). 

5. Sadalamulidwe (china) koma 
kuti Ampembedze Mulungu 
(mmodzi yekha) Ndikuyeretsa 
chipembedzo Chake Popendekera 
ku choona (ndi kusiya njira Zonama) 
ndi kuti asunge Swala ndiponso 
Apereke chopereka (cha pachuma 
chawo); chimenecho (Ndicho) 
chipembedzo choongoka. 3 

6. Ndithu, amene 
sadakhulupirire (Mneneri) (SAW) 
Pakati pa anthu a mabuku ndi 












1 Tanthauzo la "Makalata oyeretsedwa kuzonama" ndi Qur'an. 

2 Kapena kuti "mkati mwake muli mabuku olingana," ndiye kuti m'Qur'an muli 
zophunzitsa za mabuku onse omwe Mulungu adavumbulutsa kwa Aneneri 
onse akale. 

3 Tanthauzo lake ndikuti "Mneneri uyu" sadadze ndi chinthu cha chilendo 
chakuti ndikumukanira. Koma iye akulamula za kupembedza Mulungu 
Mmodzi ndi kumuyeretsera chipembedzo Chake; kuima ndi kupemphera, 
kupereka chopereka etc. Zoterezi ndizonso adali kuphunzitsa aneneri onse 
omwe adadza ndi zipembedzo zoongoka. 



Surat 99. Az-Zalzalah Juzu 30 



1383 r*ij±\ 



^ * aijjjji Sj^ 



opembedza Mafano 
adzalowetsedwa ku Jahannama 
Ndikukhala m'menemo muyaya; 
iwowo ndiwo Zolengedwa zoipa. 

7. Ndithu, amene akhulupirira 
(mwa Mulungu ndi Mthenga 
Wake) ndikumachita zabwino, Iwo 
ndiwo zolengedwa zabwino. 

8. Malipiro awo kwa Mbuye 
wawo, Ndi minda yamuyaya 
momwe Ikuyenda pansi pake 
mitsinje; adzakhala M'menemo 
muyaya. Mulungu adzalandira 
ntchito Zawo nawonso adzayamika 
zabwino Zake ndi 
Kukondweretsedwa nazo (zomwe 
adzawapatse); Zimenezo ndi za 
yemwe awope Mbuye wake 
(Mulungu). 



^ijjsjKajj 










Ma aya a surayi akulongosola za tsiku lomaliza monga 
kugwedezeka kwa nthaka, kutuluka akufa ndi zomwe zidali 
mkati mwanthaka, kudabwa munthu ndi kudzifunsa yekha 
modzidzimuka, ndi anthu kuchoka mmanda mwawo kuti 
akalandire mphoto zawo. 



Surat Az-Zalzalah XCIX 



\mm 



^Xi&jMc V 



:£_ 



g3JR5«.S| 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Likadzagwedezedwa dziko 



Q^lt^l^U 



-^ 



®W;J>«j#i 



Surat 99. Az-Zalzalah Juzu 30 



1384 



*j* 



S ^ iJjljJl 5j^ 



Lapansi kugwedezeka kwake 
Kwamphamvu 

2. Ndipo nthaka idzatulutsa 
mitolo Yake (zinthu zomwe zidali 
mkati Mwake, monga akufa ndi 
miyala Yamtengo wapatali), 

3. Ndipo munthu adzanena 
(mwa mantha, Ndikudabwa nthawi 
imeneyo) Ha! Yatani nthaka,(kodi 
Kiyama yafika)? 

4. Tsiku limenelo idzanena 
nkhani Zake zonse, (zabwino 
kapenaZoipa). 1 

5. Pakuti Mbuye wako 
adzailamula Kutero (kuti 
igwedezeke ndikunena Zimene 
zinkachitika pamwamba pake). 

6. Tsiku limenelo anthu 
adzachoka (M'manda) ali 
mmagulu obalalika kuti 
Akasonyezedwe ntchito zawo 
(ndikudziwa Chiwerengero chawo 
chimene Chili kwa Mulungu). 



1 Idzanena nthaka pa tsiku limenelo pamene Mulungu adzaiuza kuti inene 
monga momwe amazinenetsera zinthu zimene chikhalire sizilankhula, pakuti 
Mulungu ndi wamphamvu zonse. 

Kapena m'mene iti idzakhalire nthaka kudzakwanira munthu kudziwa kuti 
ikutanthauza chakuti, popanda kutulutsa mawu monga momwe timadziwira 
munthu wosangalala ndi chisoni; wanjala ndi wokhuta popanda 
kulankhula. Nkhani zomwe idzafotokoza nthaka pa tsiku limenelo, monga 
momwe adanenera Mneneri Muhammad (SAW), ndi izi> 
Tsiku la chiweruzo nthaka idzamuikira umboni munthu aliyense kapena 
m'badwo uliwonse pa chimene adachita pamwamba pake (pamwamba pa 
nthaka). Limeneli ndilo tanthauzo la mawu aja oti " Nthaka idzanena nkhani 
zake." 



© UjU»J e>^si v^4jj. 






Surat 100. A1-' Adiyat Juzu 30 1385 r * ^jA-i 1 • * obMaJi 5^ 



7. Choncho, amene angachite 
chabwino Cholemera ngati kanjere 
Kakang'ono, adzaona malipiro 
ake. 1 

8. Ndipo amene angachite 
choipa Cholemera ngati kanjere 
Kakang'ono, adzaona malipiro 
ake. (Mulungu sachitira chinyengo 
aliyense). 










SURAT AL-'ADIYAT C 

n^_ ^m 




Kumayambiriro a surayi Mulungu wolemekezeka walumbirira 
akavalo omenya nkhondo kuti ndithu, munthu ali wokanira 
kwambiri pamtendere wa Mbuye wake, (Mulungu). Ndithu, iye 
mwini adzaikira umboni pazimenezi tsiku lomaliza, ndikuti iye 
pokonda chuma ali wa msulizo. Ndipo kotsirizira kwake 
yafotokoza za kuuka ndi kuweruzidwa pa tsiku lomaliza. 



Surat Al-' Adiyat C 



— -"~" 



m mm&t 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikulumbirira akavalo 
Othamanga ali ndi phuma, 

2. Ndiotulutsa moto kuzikhotwa 
(Pomenyetsa miyendo m'miyala), 

3. Ndiothira nkhondo adani 
Mmawa (dzuwa lisadatuluke); 



0&£\<£®\&\j 



^ 






1 (Ndime 7-8) Ma aya awiriwa akutidziwitsa kuti munthu adzalipidwa pa 
chilichonse chimene akuchita, chabwino kapena choipa, ngakhale chikhale 
chochepa monga kulemera kwa kanjere kochepa kwambiri. 



Surat 100. Al- 4 Adiyat Juzu 30 1386 1" . *>! > • • olouJi 5^ 



4. Ndikuulutsa fumbi lambiri 
(Kwa adani) nthawi imeneyo, 

5. Ndikulowerera mkatikati 
mwa Adani. 

6. Ndithu, munthu ali wokanira 
Mbuye wake, (Sathokoza Mulungu 
pazimene Amdalitsa nazo). 1 

7. Ndithudi iye pazimenezi ndi 
Mboni (yozichitira yekha 
Kupyolera mzochitachita zake). 

8. Ndipo ali wokonda chuma 
Kwambiri (ndiponso 
ngwamsulizo). 

9. Kodi sakudziwa 
zikadzatulutsidwa Za m'manda; 

10. Ndikudzasonkhanitsidwa 
Ndikudzaonekera poyera zomwe 
Zidali m'mitima? 

11. Ndithu tsiku limenelo 
Mbuye wawo Adzawadziwa 
kwambiri (Ndikuwalongosolera 
zonse zochita zawo). 






<3S$<3^MS& 



uCud^^il Sr^vlj 









1 Tanthauzo la "kukanira Mbuye wake" ndi kuukanira mtendere Wake. Ndipo 
kukanira mtendere ndiko kusagwiritsira ntchito mtenderewo mnjira zabwino, 
monga m'mapemphero ndi zina zotero. 

2 Kapena kuti ali wofunitsitsa chuma kwambiri; kumeneko ndikumangoti 
mtima dyokodyoko pachuma. Ukachipeza ndikumachichitira umbombo ndipo 
ndikumaganiza kuti chumacho nchopambana china chilichonse. 

3 "Kuwadziwa kwambiri," kukutanthauza kuti lye ngodziwa zazikuluzikulu ndi 
zazing'onozing'ono zoonekera poyera ndi zobisika. Tsiku limenelo 
adzawalipira chilichonse chimene adachita. 



Surat 101. AI-Qari'ah Juzu 30 1387 f * *>i 1*1 apjUil 5^ 




Surayi yayamba ndikuopseza kwa kugunda kwamphamvu 
komwe kudzagonthetsa makutu a anthu pa tsiku la kutha 
kwadziko. Ndipo yalongosola machitidwe ena a tsiku limenelo a 
anthu ndi mapiri. Ndiponso yalongosola za amene zabwino zawo 
zidzalemera pa sikelo ndikupepuka zoipa zawo. 



Sural Al-QarVah CI 






l mm 



&m\K?A 



,*: 



t'%\ 



o£*3\^3\&\j 



-*£ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kugunda kwa phokoso (la 
Kiyama)! 

2. Kodi kugunda kwa 
phokosolo Ndi chiyani? 

3. Ndichiyani 
chingadzakudziwitse za Kugunda 
kwa phokoso (la Kiyama Komwe 
kudzawakomole anthu)? 

4. Limenelo ndi tsiku limene 
anthu Adzakhala ngati agulugufe 
Obalalika, 

5. Ndipo mapiri adzakhala ngati 
Ubweya opakidwa penti, 
womwazidwa (Wongouluka uku 
ndi uku mumlengalenga). 



1 Apa, pakutanthauza kuti anthu adzakhala ali balalabalala ngati agulugufe 
ndipo azidzangodziponya uku ndi uku, osadziwa kopita. Imeneyo ndi nthawi 
yotuluka m'manda. 






Surat 101. Al-Qari'ah Juzu 30 1388 ? * *>» \0 *pjUJi ojj- 



6. Tsono amene muyeso wake 
(wa zinthu Zabwino) udzalemere 
(ndikupepuka Zoipa). 1 

7. Ndiye kuti iye adzakhala mu 
umoyo Wosangalatsa (patsiku 
lachiweruzo). 

8. Ndipo yemwe muyeso wake 
(wa zinthu Zabwino) udzapepuka 
(ndi kulemera Zoipa), 

9. Ndiye kuti mbuto yake ndi ku 
Hawiya. 

10. Kodi ndi chiyani 
chingakudziwitse Za Hawiya? 

11. Umenewo ndi mo to woyaka 
mwaukali! 



via ■* immtm lu,u 



^.^■wtffc 









kk£& 



l SURAT AT-TAKATHUR CII 




Surayi ikudzudzula aliyense wosiya malamulo a Mulungu 
chifukwa chotanganidwa ndi zamdziko. Ndipo yawachenjeza kuti 
adzadziwa zotsatira za kunyozera kwawo malamulo a Mulungu 
pamene adzauona moto masomphenya ndikufunsidwa za 
mtendere uliwonse umene Mulungu adawadalitsa nawo kuti 
adauchitira chiyani. 



1 Tsiku limenelo ntchito zonse zabwino ndi zoipa zidzayesedwa ndi muyeso 
wa Mulungu, koma sitidadziwitsidwe kuti muyeso umenewo udzakhala wotani 
udzayesa zonse zazikulu ndi zazing'ono zomwe mpaka za mumtima. 



Surat 102. At-Takathur Juzu 30 



1389 r. *>» i.ryiUiSjj-, 



Surat At-Takathur CII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kwakutangwanitsani 
kusonkhanitsa Chuma chambiri 
ndi wana. 1 

2. Mpakana mwapita kumanda 
(Mwamwalira ndikukalowa 
Mmanda). 

3. Sichoncho! mudziwa 
posachedwapa. 2 

4. Ndiponso sichoncho! 
Mudziwa Posachedwapa. 

5. Sichoncho! mukadakhala 
mukudziwa, Kudziwa 
kwachitsimikizo (sibwenzi 
Mukutangwanika ndi zamdziko). 

6. Ndithudi mudzauona moto, 

7. Kenako mudzauona ndithu 
ndi diso la Chitsimikizo. 

8. Tsono patsikulo ndithudi 
mudzafunsidwa 3 



4'i 



1 



O&rgS^&J 



-& 



&5^il'- 






®u^^y^<I>! 






1 (Ndime 1-2) Ndi chizolowezi cha anthu kupikisana pa chuma ndi pa ana. 
Choncho, mma aya awa: 1-2 Mulungu akuwauza: Kupikisana kwawo 
kochuluka, kukonda za m'dziko kwambiri, kwaiwalitsa kutumikira Mulungu 
mpaka imfa kuwapeza. 

2 Tanthauzo lake ndilakuti, pamene idzakufikirani imfa mudzadziwa kuti 
mudali kutaya nthawi ndi zinthu zopanda pake. 

3 Munthu aliyense ndi chilichonse chimene ali nacho ndi mphatso yochokera 
kwa Mulungu. Choncho, pa tsiku lomaliza adzafunsidwa za momwe 
adagwiritsira ntchito mphatso zimenezi, kaya m'njira yoipa kapena yabwino. 



Surat 103. Al-'Asr Juzu 30 



1390 



*>' 



S • T j~f*"b\ *JJ** 




Mulungu Wolemekezeka akulumbirira nthawi msurayi 
chifukwa chakuti nthawi yasonkhanitsa zodabwitsa zambiri mkati 
mwake, zomwe ndi maphunziro kwa anthu olingalira, zomwenso 
zikusonyeza mphamvu za Mulungu ndi luso lake pa chilichonse, 
kamba ka nthawi , munthu salekana ndi kuchepekedwa ndi 
kusintha m' ntchito zake ndi makhalidwe ake, kupatula 
okhulupirira amene amachita zabwino ndikumalangizana pakati 
pawo kugwiritsa choona cha Mulungu, ndikulangizana za kupirira 
pazimene alamulidwa kuzitsata ndi kupewa zomwe aletsedwa 
kuchita. 



Surat Al-'Asr CHI 



m^smm'JM 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndikuilumbirira nthawi. 1 

2. Ndithu, munthu aliyense ndi 
Wotaika (chifukwa 
chakugonjetsedwa Ndi zilakolako 
zake), 

3. Kupatula amene akhulupirira 
(mwa Mulungu) ndi kumachita 
zabwino, Ndikumalangizana 
kutsatira choona Ndiponso ndi 
kumalangizana za Kupirira 
(potsatira malamulo A Mulungu 



QWH^* 



-^ 









Chinthu cha mtengo wapatali kwa munthu padziko lino ndi moyo wake. 
Choncho mphindi iliyonse imene akuigwiritsa ntchito pa zinthu zabwino ndiyo 
imene idzamuthandiza. Ndipo mphindi iliyonse imene akuigwiritsa ntchito mu 
zinthu zoipa kapena zopanda pake, kumeneko ndiko kutaika kwake; (kuluza). 



Surat 104. AI-Humazah Juzu 30 



1391 r. *>i 



^ « £ 3j*Al Ojj— i 



ndi zina zovuta za mdziko). 



JESp^™"""""^'""""" ' """"" 

[T SURAT AL-HUMAZAH CIV 




M'surayi muli lonjezo la chilango choopsa kwa munthu amene 
ali ndi chizolowezi chojeda ndi kunyoza anthu, powalozera ndi 
maso kapena kulankhula. Ndiponso amene amati akasonkhanitsa 
chuma amachiwerengera pafupipafupi mokhumbiza ena uku 
akuganizira kuti chumacho chimkhazika muyaya. 



Surat Al-Humazah CIV 



# mm 



_____ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kuonongeka koopsa 
kudzampeza Aliyense wojeda ndi 
wonyoza Anthu polozera (ndi maso 
kapena Kuyankhula ndi lirime), 2 



oj&3\^3\&\j 



-+± 






Mgulu la otaika mwapatulidwa anthu olungama amene zochita zawo zili 
zolungama, omwe amalamulira kutsatira njira yolungama ndi kupirira. Anthu 
otere saataika, chifukwa chakuti nthawi yawo amaigwiritsira ntchito pa zinthu 
zabwino, zowathandiza padziko ndi pambuyo pa imfa. 
Kupirira kulipo mitundu inayi:- 

(a) Kupirira pochita zinthu zabwino zomwe zili zovuta kwa munthu kuzipitiriza, 
monga kupemphera swala zisanu. 

(b) Kupirira posiya kuchita zoipa zimene zili zovuta kwa munthu kuti azileke. 

(c) Kuwapirira anthu anzako; kupirira ndi zoipa zawo posawabwezera choipa 
chilichonse. 

(d) Kupirira ndi mazunzo a padziko, monga njala, matenda, kusauka ndi zina 
zotero. 

2 Kujeda kwa mtundu uliwonse ndi koipa. Anthu ambiri amaganiza kuti kujeda 
ndi chinthu chochepa, saona kuti ndi chinthu choipa, pomwe Qur'an ikuletsa 
kwatunthu mpaka mwakuti imamufanizira munthu wojeda ngati munthu 
yemwe amadya minofu ya mnzake wakufa. Mu aya imeneyi, Mulungu wanena 
kuti "Wayilun" lomwe tanthauzo lake ndi "Kuonongeka koopsa." Choncho 
nkofunika kwa munthu aliyense kupewa khalidwe lojeda. 



Surat 104. AI-Humazah Juzu 30 



1392 



*>' 



y • t Sj^ii 3jj^ 



2. Yemwe wasonkhanitsa 
chuma Ndikumachiwerengera. 1 

3. Akuganiza kuti chuma 
chakecho Chimkhazika (padziko) 
muyaya (Ndikumteteza kuzimene 
sakuzifuna). 

4. Sichoncho! (asiye maganizo 
amenewo) Ndithudi, akaponyedwa 
ku Moto woononga (chifukwa cha 
kuipa Kwa zochita zake). 

5. Ndi chiyani 
chingakudziwitse Za moto 
woonongawu? 

6. Umenewu ndi moto wa 
Mulungu woyaka (Nthawi zonse, 
woononga chilichonse 
Choponyedwa mmenemo); 

7. Umene umakwera mpaka ku 
mtima. 2 

8. Ndithu, motowo ukawazinga 
(ndi Kuwatsekera makomo); 

9. Munsanamira za zitalizitali 
(Kotero kuti sakatha kugwedezeka 
Mmenemo kapena kupulumuka). 






ft£&\$&S®$ 



®k&&&iffi> 



©*JsjtfUfc!$ 






Mmenemo ndi momwe alili munthu wa umbombo, kukoma kwa chuma kwa 
iye, ndikuchisonkhanitsa ndikumachiwerengera akakhala ndi danga; sikuti 
akufuna kudziwa kuchuluka kwake koma kungokondweretsedwa 
ndikuchiwerengako. Saganizira zimene zingamuthandize iye mwini kapena 
kuthandiza anzake. 

Chuma ntchito yake ndikuti chimthandize mwini chumacho pa zinthu zabwino 
zosiyanasiyana pamodzi ndi anzake, osati kungochikhazika 
ndikumangochiwerengera mokhumbiza ena. 

2 Moto umenewu, sukapsereza kunja kokha, ukapsereza mpaka ndi mumtima 
momwe. 



Surat 105. Al-Fil 



Juzu 30 



1393 



r* *>» 



\ * O J-jlJl 5jj~* 




SURAT AL-FIL CV 



— -,- 




Mulungu akulongosolera Mtumiki Wake nkhani ya eni njovu 
amene adafuna kugumula nyumba ya Mulungu. Ndipo 
akumsonyeza phunziro limene lili m'nkhaniyi lomwe likusonyeza 
ukulu wa mphamvu za Mulungu kudzanso chilango Chake kwa 
amene akunyoza zinthu Zake zopatulika. 

Ndithu, Mulungu adawatumizira magulu ankhondo amene 
adawaonongeratu kwatunthu kotero kuti matupi awo adakhala 
ngati udzu wodyedwa ndi nyama kapena gaga wambewu 
zoonongedwa ndi tizilombo. 



Surat Al-Fil CV 



; $M$ M 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kodi sudaone momwe 
Mbuye wako Adawachitira eni 
njovu? 1 



(W^9i^ 



~w 



&$U^eg55 <3&$ 



1 Sura imeneyi ikufotokoza mbiri imene idachitika pafupi ndi mzinda wa Makka 
mchaka cha 570 A.C. Dziko la Yemen lidali kulamulidwa ndi anthu a mtundu 
wa Ahabashi (ochokera ku Ethiopia). Iwowo pa nthawi imemeyo adali 
Akhristu. Bwana Mkubwa (Gavanala) waku Yemen pa nthawiyo adali Abraha. 
Abrahayu adafuna kuwaletsa Arabu kuti asamapite ku Makka kukayendera 
Kaaba. Pa chifukwa ichi adamanga tchalichi lalikulu kwambiri ndiponso 
lokongola lomwe lidali mu mzinda wa Sanaa. Adawakakamiza Arabu 
kuyendera tchalichilo m'malo mopita ku Al-Kaaba Pamene Arabu adamva 
zimenezi zidawanyansa. Ndipo adadza munthu wina wochokera ku fuko la 
Kanaani ndikukalowa m'tchalichimo ndikuchitiramo chimbudzi. Adatenga 
chimbudzicho ndikupakapaka m'zipupa za tchalichi lija chifukwa 
chonyansidwa ndi nyumbayo kuti siidali yoyenera kulowa m'malo mwa Kaaba. 
Pamene adaona izi, Abraha adakwiya kwambiri ndipo adalumbira kuti 
sachitira mwina koma kukagumula Kaaba. Adasonkhanitsa gulu la nkhondo 
lalikulu momwe mudalinso njovu zakuti zikamthandize kugumula Al-Kaaba. 
Choncho adauyatsa ulendo kupita ku mzinda wa Makka. 
Abraha pamene adafika ku Makka, adatumiza munthu kwa Arabu kuti 



Surat 105. AI-Ftl Juzu 30 1394 r * *>i 



\ ♦ O J-ji3l Ojj-j 



2. Kodi sadachichite chiwembu 
Chawo kukhala chosokera 
(Chopanda phindu?) 

3. Adawatumizira 
magulumagulu a Mbalame 
otsatizana. (ndipo Adawazungulira 
mbali zonse;) 

4. Zimawagenda ndi miyala ya 
moto; 

5. Adawachita ngati m'mera 
wodyedwa (ndi Nyama ndi 
kulavulidwa). 



s^a;*^'-'' 1 



0^JjT!^>^ J^Ij 



<i \^&jfJ^ > HA? 



®djtfLx&^&>6 



awafotokozere kuti iye sadadze kudzawathira nkhondo, koma adadzera 
kudzagumula Al-Kaaba. Choncho adawapempha kuti amupatse danga kuti 
atero. Abdul Mutwalib adalamula anthu ake onse kuti achoke mu mzindawo 
apite ku mapiri.lye adakalowa Mnyumba ya Kaaba ndipo adapempha 
Mulungu kuti ayipulumutse nyumba Yake yopatulika. Kenaka nayenso 
adawatsatira anzake ku mapiri kuja ndipo adangokhala phee, kuti amuone 
bwino yemwe adali kulimbana ndi Mulungu pomugumulira nyumba Yake. 
Abraha pamene adadziwa kuti Arabu atuluka mu mzindamo adakonzeka 
kulowa m'Makka ndi kugumula AL-Kaaba. Koma Mulungu Wamphamvu 
zonse adamutumizira gulu Lake la nkhondo monga momwe mukuwerengera 
pa aya yachitatu. Ankhondo a Abraha ena adafera pompo koma ena 
pamodzi ndi iye mwini, adathawa ndikukafera kwawo ku Yemen. Pa chifukwa 
chimenechi Arabu ankachitcha chaka chimenechi kuti "chaka cha njovu." 
Choncho mwana aliyense wobadwa m'chakachi ankatchedwa mwana 
wobadwira m'chaka cha njovu. Ndipo Mneneri Muhammad (SAW) adabadwa 
m'chaka chimenechi ndipo ankadziwikanso monga mwana wobadwa m'chaka 
cha njovu. 



Surat 106. Quraish Juzu 30 



1395 



*>' 



> • 1 J* J °Jf 




M'surayi Mulungu akufotokoza za mtendere Wake umene 
udali pa Aquraish powadalitsa ndi nyumba Yake yopatulika 
imene adali kuiteteza kwa adani Ake. Adawakhazika mmbali 
mwake ndipo adapeza ulemerero ndi mtendere. 

Amayenda nthawi ya chirimwe kupita ku Sham ndipo nthawi 
ya dzinja amapita ku Yemen ndikumakachita malonda 
mwamtendere popanda chowapinga chilichonse, pomwe anzawo 
adali kufwambidwa. 

Chimenechi ndi chisomo chofunika kuchiyamika, ndi 
kumpembedza amene adawachotsera njala ndi mantha. 



Surat Quraish CVI 






,n m » 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Cholinga chakuwachita 
MaQuraish Kuti apitirize 
chizolowezi chawo, 1 



Q^^t^jM«&U- 



©, 



\&^m 



(Ndime 1-4) Al-Kaaba, ndidzachidziwikire kuti, adali malo opatulika kwa 
Arabu onse kuyambira nyengo ya Ibrahim (Abraham) (AS) yemwe adamanga 
nyumbayi potsatira lamulo la Mulungu. Aquraish amene ankasunga ndi 
kuyang'anira nyumba yopatulikayi, adali kupatsidwa ulemu ndi Arabu ena 
onse. Ndipo pa chifukwa chimenechi adali kutha kuyenda ulendo wopita ku 
Yemen nthawi ya dzinja, ndiponso ku Sham nthawi yachirimwe kukachita 
malonda ndikubwerera bwinobwino. Sadali kuputidwa ndi achifwamba m'njira, 
pophedwa kapena kulandidwa chuma chawo momwe ankachitiridwa Arabu 
ena. 

Pamene idamveka nkhani ya njovu.kulemekezedwa kwawo kudaonjezeka 
kuchokera kwa mitundu yonse ya Arabu. Mu sura imeneyi, Mulungu 
akuwakumbutsa za madalitso amenewa ndiponso akuwauza kuti 
adawafewetsera kayendedwe ka maulendo awo nthawi ya dzinja ndi chilimwe 
kuti akachite malonda ndikupeza chakudya ndi zina zofunika pa moyo wawo. 
Adawapatsa chitetezo posakhala ndi mantha m'njira; mantha omwe mitundu 



Surat 106. Quraish Juzu 30 1396 ? * *>' 



> * t J*lJ 5 JJ-" 



2. Apitilize chizolowezi chawo 
choyenda Nthawi ya dzinja 
(kunka ku Yemen) Ndi nthawi 
yachirimwe(kunka Ku Sham 
kukachita malonda, 
Mosatekeseka ndi mopanda 
mantha). 

3. Choncho, amupembedze 
Mbuye wa Nyumba iyi (Al-Kaaba 
amene Adachititsa kuti athe 
kuyenda Maulendo awiriwo); 

4. Yemwe amawadyetsa 
(nthawi imene Arabu anzawo) ali 
m'njala, Amawapatsa chitetezo 
(pomwe Anzawo) ali ndi mantha. 



h^\fy^M 



%Q\^Ci>\jo^ 







Surayi ikukamba za otsutsa tsiku la malipiro limene lili tsiku 
lomaliza. Ndipo yalongosola mbiri zawo motere: lye ndi yemwe 
amapondereza ana amasiye ndikuwakalipira mwankhanza, osati 
kuwalangiza miyambo yabwino. Iyenso ndi yemwe 
samalimbikitsa ena ndi mawu kapena ndi ntchito zake monga 
kudyetsa osauka chifukwa iye ndi woumira pazimene alinazo 
mmanja. Kenako yatchula gulu lofanana ndi wotsutsa tsiku 
lamalipiro. Iwowa ndi amene akuchitira mphwayi mapemphero 
awo. Sachita mapemphero awo moyenera, koma akuwachita 



ina ya Arabu idali nawo. Madalitso onsewa ankawapeza chifukwa cha 
nyumba ya Al-Kaaba. Choncho kudali koyenera kwa iwo kumupembedza 
Mwini nyumbayo, osati mafano. 

Pakadapanda nyumba Yakeyo sakadatha kumayenda maulendo mwa 
chitetezo, ndiponso sibwenzi kukudza aliyense ku mzindawo (Makka) 
chifukwa mukadakhala mulibe chodzetsa alendo 



Siirat 107. Al-Ma'un Juzu 30 1397 T * *> 



> * V O^Plll 9jj*> 



monga chithunzi chopanda tanthauzo. Amangoonetsera zochita 
zawo kwa anthu. Amamana osowa chithandizo chawo. Ndipo 
sura iyi ikuwalonjeza chilango ndikuonongeka kuti asiye 
machitidwe awowo. 



Surat Al-Ma'un CVII 



: i -. 



mmmz 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Kodi wamuona yemwe 
akutsutsa Za mphoto (ndi 
chiwerengero Cha tsiku 
lomaliza)? 1 

2. lye ndi yemwe akukankha 
wamasiye (Mwankhanza). 

3. Ndipo salimbikitsa (ena 
pamodzi ndi lye mwini) kudyetsa 
osauka. 

4. Choncho kuonongeka kuli pa 
Ena mwa opembedza (amene ali 
Ndi mbiri izi): 

5. Omwe amachitira mphwayi 
mapemphero Awo. 2 



oM^^3\^W 



&^M&3i 



fy$Kc$&i* 



%&^¥<P& 



wm 



^u^s^ 



Sura imeneyi ikufotokoza m'mene alili makhalidwe awanthu ambiri, 
ngakhale amene amadzitcha kuti ndi Asilamu. Aliyense amene ali ndi 
makhalidwe otere ndiye kuti sakhulupirira za tsiku la chiweruzo. Akadakhala 
kuti akukhulupirira za tsikuli, sibwenzi akusiya kuwachitira za chifundo 
osauka ndi amasiye. Sapereka chithandizo ngakhale kulimbikitsa ena ngati 
iye alibe. 

Kuchitira mphwayi mapemphero (swala), kumeneku ndiko kupemphera uku 
maganizo ali kwina, kapena kupemphera modukizadukiza. Tsiku lina 
nkupempherapo, tsiku lina ayi. Kapenanso kupemphera modzionetsera kwa 
anthu (riyaa). 



Surat 107. Al-Ma'un Juzu 30 



1398 



*>' 



) * V dj*&\ 9jj~> 



6. Amenenso (akamachita 
mapemphero Awo) 
amadzionetsera (kwa anthu 
Mwachipha maso kuti apeze 
ulemerero Ndi kutamandidwa 
mmitima mwa anthu); 1 

7. Ndipo amamana ziwiya 
(zawo posabwereka Anzawo 
zinthu zofunika pa moyo wa 
Aliyense monga nkhwangwa, 
mpeni, Mtondo ndi zina zotere). 



&, 



>&%&& 



s->9K'\i'*9' , >" 



t&**# 




SURAT AL-KAUTHAR CVIII 



^_ 




M'sura imeneyi Mulungu akutchula ufulu Wake umene 
adamchitira Mneneri Wake (SAW) pompatsa zabwino zambiri 
ndi chisomo chachikulu pano padziko ndi tsiku lomaliza. Ndipo 
wamuuza kuti apitilize kupemphera swala yake ncholinga 
chofuna chikondi Chake osati china ayi. Ndiponso akumuuza kuti 
aphe nyama ya nsembe imene ili yodalirika mchuma chake 
posonyeza kuthokoza pazimene Mulungu wampatsa monga 
ulemerero waukulu. 

Ndipo sura imeneyi yamaliza ndi nkhani yakudukidwa 
mwawi wa mdani wake amene adali kuda Mtumiki (SAW) 
kwambiri ndikumamutcha kuti ngopanda mwawi. 



Riyaa ndiko kuchita ntchito yabwino ndicholinga choonetsa anthu, kuti 
akuone kuti ndiwe wabwino, mwina kuti ukhale wokondedwa ndi anthu. 
Kapenanso kuti upeze za m'matumba mwawo. Amenewa ndi machitidwe a 
"Shiriki " (Kum'phatikiza Mulungu ndi zolengedwa Zake pa mapemphero) 
Ndiponso, ndi njira yobera anthu. 



Surat 108. Al-Kauthar Juzu 30 I 1399 I T . s-jA-i \ . A jJj&i t ir > 



Surat Al-Kauthar CVIII 





.3? — — ^- 


. ^r^J^=3- / <^LCLiA \ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Ndithu, takupatsa zabwino 
Zambiri (zina mwa izo ndi Mtsinje 
wotchedwa Kauthar). 1 

2. (Pakuti ndakupatsa 
zimenezo), Pitiliza kupembedza 
Mbuye wako (Moyera mtima) 
ndipo ipha nsembe yako 
(Chifukwa chakuthokoza Mulungu 
Pazimene wakupatsa, monga 
Ulemerero ndikukusankhira 
Zabwino zambiri). 2 

3. Ndithu, mdani wako Ndiye 
ali wopanda mwawi. 



Q^Jlfc^J)!^ 



-a 



©^atf'' 1(? < 



*&£&& 



%#}£&&& 



Tanthauzo la "zabwino zambiri" apa, ndi uneneri, maphunziro, ntchito 
zabwino, ulemerero, kupambana pakukhala ndi omutsatira ambiri ndi zabwino 
zina zam'dziko lino lapansi ndi tsiku lomaliza, zosawerengeka zomwe 
sadapatsidwe aliyense pambuyo pa iye ngakhale mtsogolo mwake. Ndithu, 
zimenezi, popanda chikaiko, ndizabwino kwambiri kuposa chuma ndi ana. 

2 Tanthauzo loti "Mbuye wako yekha umupembedze" kuti amupembedze 
Mulungu yekha, asachite chiphamaso, asakhale monga amene amachita 
mapemphero ndi cholinga choti adzionetsere kwa anthu. Ndikutinso apereke 
nsembe m'dzina Lake, osati azimu ndi zina zotero. 

3 Yemwe akukunena iwe kuti ndiwe wodukidwa ndi mwawi, sichoncho, koma 
iyeyo ndiye ali wodukidwa ndi mwawi, pakuti iwe takupatsa zabwino zambiri , 
osafanana ndi iye ngakhale kuti iye ali ndi chuma ndi ana. 

Adani a Mtumiki (SAW) adali kukondwera kwambiri pamene ankaona kuti ana 
ake onse achimuna atha kumwalira, iwo ankaona kuti palibe ubwino uli onse 
kwa munthu pano padziko ngati sadapatsidwe ana achimuna ndi chuma. Pa 
chifukwa ichi, adali kumutcha "Abutaru," wopanda madalitso. Msura imeneyi 
Ambuye Mulungu akumtonthoza Mneneriyo ndiponso akuyankha adani ake. 



Surat 109. Al-Kafirun Juzu 30 I 1400 I T • *>» \ * S Ojjdi&i 5jj~- 




M'sura imeneyi Mulungu akulamula Mneneri Wake kuti 
awauze okanira (osakhulupirira) kuti sipadzapezeka chimvano 
pakati pa iye ndi chipembedzo chake choona ndi pakati pa iwo 
ndi chipembedzo chawo chabodza. Koma iye adzapitiriza 
kupembedza Mulungu amene palibe wina wopembedzedwa 
mwachoonadi koma Iye. Ndipo naonso adzapitiriza kupembedza 
mafano awo omwe sangathandize chilichonse. 



Surat Al-Kafirun CIX 



\mmm 

fcCi — 



':( 



^g= , , _JJ 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nena (iwe Mtumiki) (SAW): 
Ee'.InuAnthu osakhulupirira! 1 

2. Sindipembedza chimene inu 
Mukuchipembedza (kusiya 
Mulungu). 

3. Inunso simumpembedza 



ojk£\<&$\&\jr 



h&^K$&$ 



© <jj&^joU> jJ^l^f 






1 (Ndime 1-6) Osakhulupirira a mu mzinda wa Makka pamene adaona kuti 
atopa, sangathe kuzimitsa dangalira la Usilamu ndipo adamuona Mneneri 
(SAW) tsiku lililonse akuonjezera khama pa ntchito yake, chipembedzo nacho 
chikunkerankera mtsogolo, adapempha Muhammad (SAW) kuti pakhale 
chimvano pakati pa iwo ndi iye choti amupembedze Mulungu wa Mneneri 
(SAW) chaka chimodzi pamodzi naye, nayenso pa chaka chinacho 
asanganikirane nawo popembedza milungu yawo chaka chimodzinso. 
Kumeneku ndiko kuti chaka, apembedze Mulungu wa Mneneri (SAW), 
nayenso apemphere milungu yawo chaka chinacho. Apa ndipo pamene 
idavumbulutsidwa surayi. Cholinga chake ndi ichi: Inu muli ndi milungu 
yanu, inenso ndili ndi Mulungu wanga. Sizingatheke kusanganikirana pakati 
pa milungu yanu yonama ndi Mulungu wanga woona, ngakhalenso ndi 
mapemphero anu onama ndi mapemphero anga oona. Inu muli ndi 
chipembedzo ndichikhulupiriro chanu, inenso ndili ndi chipembedzo ndi 
chikhulupiriro changa. 



Surat 109. Al-Kafirun Juzu 30 



1401 



r * ^jA-i ^ * * o ^i&i 5^^ 



amene ine Ndikumpembedza 
(yemwe ndi Mulungu mmodzi). 

4. Ndiponso ine 
sindidzapembedza Chimene inu 
mwakhala mukuchipembedza 
(Chifukwa inu ndinu ophatikiza 
Mulungu ndi zinthu zina). 

5. Ndipo inu 
simudzampembedza Amene ine 
ndikumpembedza (Yemwe ndi 
Mulungu mmodzi) 

6. Inu muli ndi chipembedzo 
chanu (Chimene 
mkuchikhulupirira), Inenso ndili 
ndi chipembedzo Changa (chimene 
Mulungu Wandisankhira). 



©^sJl^Ij; $J*&\yj 



®u^llit^JLi>ol^ 



&&}'&&& 




SURAT AN-NASR CX 




Surayi ikumuuza Mtumiki (SAW) kuti chikadza 
chipulumutso cha Mulungu ndikugonjetsa Makka, ndikutinso 
akaona anthu akulowa mchipembedzo cha Mulungu 
mmagulumagulu, pamenepo amulemekeze Mulungu ndi 
kumyamika ndi kumyeretsa kuzinthu zosayenera kwa lye. 
Ndikutinso ampemphe chikhululuko kuti chimfikire iye ndi 
anthu ake okhulupirira. Chifukwa chakuti Mulungu 

ndiwolandira kulapa kwa anthu ake ndikuwakhululukira 
zolakwa zawo. 



Surat 110. An-Nasr Juzu 30 1402 T * *>» ) ) * j-aJ» $;>-» 



SuratAn-NasrCX 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Chikafika chipulumutso cha 
Mulungu Ndi kugonjetsa (mzinda 
wa Makka Kwa iwe ndi 
okutsatira), 1 

2. Ndi kuwaona anthu akulowa 
M'chipembedzo cha Mulungu ali 
Magulumagulu, 

3. Pamenepo lemekeza Mbuye 
wako ndi Kumtamanda ndiponso 
mpemphe Chikhululuko, ndipo lye 
ndiwolandira Mochuluka kulapa 
(kwa anthu Ake). 3 



l%& W*$& '7:^ 



o&&\<&$\&W 



*-%^j^>\ 






Hi ndi lonjedzo la Mulungu kwa Mneneri wake (Muhammad) (SAW) kuti 
amthandiza kumpulumutsa kwa adani ake amene adali kumuzunza ndi 
kufuna kumupha. Lonjezoli lidali lakuti iye adzaulamulira mzinda wa adaniwo 
momwe adamutulutsa. 

2 Mneneri (SAW) pamene adalowa mu Mzinda wa Makka ndi kugonjetsa 
adani ake monga momwe Mulungu adamulonjezera, a kafiri adali kubwera 
m'mafukomafuko kudzalowa m'chipembedzo cha Chisilamu. 

3 Tanthauzo la kuuzidwa Mneneri Muhammad (SAW) kuti zikachitika zimene 
adalonjezedwa, amulemekeze Mbuye wake, amupemphe chikhululuko, 
chikhalirecho iye adali kuchita zimenezo, izi zimatanthauza kuti moyo wake 
wayandikira kutha, watsala pang'ono kumwalira. Choncho adalamulidwa 
kuonjezera mapemphero kuti aonjezere kulinganiza tsiku lake lomaliza. 
Imeneyi ndi imodzi mwa Surah zimene zidavumbulutsidwa kotsirizira kwa 
moyo wa Mtumiki (SAW). Pamene idavumbulutsidwa Surayi, ena mwa 
maswahaba (omutsatira) adazindikira chinsinsi cha Surayi; adali kulira poona 
kuti Mneneri (SAW) amwalira posachedwa. Pambuyo povumbulutsidwa 
Surayi, Mneneri (SAW) sadakhalenso ndi moyo wautali. 



Surat 111. Al-Masad Juzu 30 I 1403 I T • *>i U 1 jUL» Sj^ 




Surayi ikulongosola za kuonongeka kwa Abu Lahabi yemwe 
adali mdani wa Mulungu ndi Mneneri Wake. Ndikuti 
pakuonongekako chuma chake kudzanso ulemerero wake 
sizidamthandize. Ndipo yamulonjeza kuti tsiku lomaliza 
adzalowa kumoto woyaka mwamphamvu ndikuotchedwa 
mmenemo. Ndiponso yamphatikiza iye ndi mkazi wake 
pachilangocho. Makamaka mkazi wake adzakhala ndi chilango 
chakechake chomangidwa chingwe mkhosi mwake 
ndikumakokedwa kumoto; kumlanga pachifukwa cha zimene 
adali kumchitira Mneneri wa Mulungu ndi kuipitsa uthenga wake. 



Surat Al-Masad CXI 



mm 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Aonongeka manja a Abi 
Lahab (Omwe adali kuwagwiritsa 
Ntchito pozunza Asilamu). 
Nayenso wawonongeka. 1 

2. Chuma chake ndi ulemerero 
wake (Umene adaupeza) 



o^l^jM^ 



■-ufl 



-r'rf *" 



&<#! 



UuC^O 



®CCZ\1aj ^3U^-(/^lU 



1 (Ndime 1-4) Pa chiyambi cha uneneri wa Muhammad (SAW) adalamulidwa 
kuti aulalikire uthenga wabwinowo kwa abale ake apafupi; adawasonkhanitsa 
ndipo adawalalikira ndi kuwachenjeza za chilango cha tsiku lomaliza. Koma 
Abu Lahab adali m'bale watate wa Mtumiki Muhammad (SAW) adakwiya 
ndipo adanena kuti "waonongeka iwe! waonongeka iwe! chimenechi ndi 
chimene watisonkhanitsira?" pa chifukwa ichi idavumbulutsidwa sura imeneyi. 
Mulungu adamubwezera Abu Lahab pamodzi ndi mkazi wake, Ummu Jamila, 
mawu otemberera. Ummu Jamila ankalimbikira kwambiri kumuzunza Mtumiki 
(SAW) ndi kuwakaikitsa amuna kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa 
kutsekereza kuti asamutsatire. Ndipo adayesetsa kutsekereza kuti Chisilamu 
chisafalikire madera ena. "Aonongeka manja wa Abu Lahab" kumeneku ndi 
kutemberera komutemberera Abu Lahab kuti aonongeke m'malo moonongeka 
Mneneri (SAW). Pakuti amene amatemberera apayu ndi Mwini Mulungu, 
ndiye kuti matemberero adamufikiradi iye. 



Suratlll.Al-Masad Juzu 30 



1404 



*j* 



^ ^ ^ JL-dl djj~* 



sizidamthandize Ku chilango cha 
Mulungu. 

3. Adzalowa ku moto wa malawi. 

4. Nayenso mkazi wake 
(adzalowa Ku moto) yemwe adali 
kusenza Nkhuni (za minga 
pomutchera Mtumiki (SAW) 
Komanso amanka nadanitsa pakati 
pa anthu). 

5. Mkhosi mwake mdzamangidwa 
chingwe Chopiringidwa bwino cha 
mlaza (Chomlanga nacho). 1 






" m 9 »<9i*' 



*k<l 



^^}ffj 




SURAT AL-IKHLAS CXII 






§ 



Ena mwa osakhulupirira adampempha Mneneri (S.A.W.) kuti 
awauze za Mulungu m'mene alili; kodi ndi wa Golide kapena 
wa siliva? Ndipo sura imeneyi idavumbulutsidwa poyankha funso 
lawo ndi kumuyeretsa Mulungu kumachitidwe a "SHIRIKI" 2 
(kumphatikiza Mulungu ndi zinthu zina). 



1 Uyu mkazi wa Abu Lahab adali wodanitsa. Ntchito yake idali kutapa mawu 
uku, kuwapititsa uku, ncholinga chofuna kusokoneza. 

2 "SHIRIKI" (Kumphatikiza Mulungu ndi zinthu zina) ili mitundu inayi: 

(a) Kukhulupihra kuti milungu ilipo yambiri monga momwe adali kukhulupirira 
akafiri a mumzinda wa Makka. 

(b) Kukhulupirira kuti alipo wina wake yemwe ali ndi mphamvu zotha kuchita 
chinthu chomwe palibe amene angachichite koma Mulungu yekha, monga, 
kuvumbwitsa mvula, kuchotsa tsoka, kudziwa za m'seri ndi zina monga izi. 
Shiriki ya mtundu uwu imapezekanso kwa anthu ena omwe amadzitcha kuti 
ndi Asilamu masiku ano. O, AMBUYE, TIPULUMUTSENI KUMACHITIDWE 
OIPAWA! 

(c) Shiriki yokhulupirira kuti pali mgwirizano pakati pa Mulungu ndi 
zolengedwa Zake zina monga momwe chilili chikhulupiriro cha Akhristu. 

(d) Kukhulupirira kuti Mulungu alinacho chofanana Naye kumbali ya 
maonekedwe Ake ndi mbiri Zake, monga momwe chilili chikhulupiriro cha 
Ayuda. 

Choncho, sura imeneyi yatsutsa zonsezi ndipo yamuyeretsa Mulungu 
kumachitidwe abodzawa. 



Surat 112. Al-Ikhlas Juzu 30 I 1405 T . *j*-i > > Y j**^ 5 J>- 



SuratAl-Ikhlas CXII 



$ ' ££& 






M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nena (Iwe Mtumiki (SAW), 
kwa amene Akukufunsa 
mwachipongwe, mbiri za Mulungu 
wako) "lye ndi Mulungu Mmodzi, 
(alibe mnzake), 

2. Mulungu ndi wokhala ndi 
zonse Wodaliridwa ndi 
zolengedwa zake. 

3. Sadabale (mwana) ndiponso 
Sadaberekedwe. 

4. Ndiponso palibe aliyense 
Wofanana ndi lye. 



o^Jll^Jll^ 



-& 



§^jUi^V. 







Surayi ikumulimbikitsa Mneneri (SAW) kuti atsamile ndi 
kufuna chitetezo kwa Mbuye wake kuzoipa zonse zochokera 
mzolengedwa Zake za Mulungu, ndi zoipa za usiku pamene 
mdima wake ukulowa pachifiikwa chakuti usiku umadza ndi 
zoipa zambiri. Ndi zoipa za afiti owononga omwe amamasula 
mgwirizano umene uli pakati pa munthu ndi mnzake kupyolera 
mmachitidwe awo a ufiti. Ndikutinso adziteteze kwa wansanje 
pamene akuchita nsanje yofuna kuchotsera anthu a Mulungu 
chisomo chimene Mulungu wawapatsa. 



Surat 113. Al-Falaq Juzu 30 1406 



*>i 



> \ r jU3i Sjj-a 



Surat Al-Falaq CXIII 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nena:ndikudzitchinjiriza Ndi 
Mbuye wam'bandakucha. 1 

2. Kuchokera ku zoipa zimene 
lye Adazilenga. 2 

3. Ndikuzoipa za usikupamene 
Mdima ukulowa mwa mphamvu. 3 

4. Ndi kuzoipa za afiti omwe 
Amauzira mu mfundo. 

5. Ndiponso ku zoipa za 
wansanje Pamene akuchita nsanje. 4 




o^i^i^u- 



-& 






1 Surayi ndi yotsatirayi, zidavumbulutsidwa nthawi imodzi. Koma pali kutsutsana; 
ena akuti zidavumbulutsidwa ku Makka pomwe ena akuti zidavumbulutsidwa 
ku Madina. Sura ziwirizi zikutiphunzitsa m'mene tingadziikire mchitetezo cha 
Mulungu, ndiponso tikuphunzitsidwa kuti lye (Mulungu) ndi mwini mphamvu 
zonse. Atha kumuteteza munthu kuchinthu chilichonse chifukwa chakuti lye 
(Mulungu) ndi Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, yemwe asiya 
chitetezo Chake ndikumafuna chitetezo cha ufiti, azimu, manda, ndi zina zotero 
ndiye kuti akuziika iye mwini kumachitidwe a "SHIRIK" (kupembedza mafano). 

2 "Zomwe adalenga" zikutanthauza chilichonse cholengedwa, chamoyo ndi 
chopanda moyo; chooneka ndi chosaoneka. 

3 Palibe chikaiko, usiku wa mdima uli ndi matsoka ambiri omwe sapezeka 
masana ndi usiku wowala. Mu usiku wa mdima, mumayenda zinthu zoopsa 
zambiri, monga zirombo zolusa, akuba, achiwembu ndi matsoka ena ambiri 
omwe tikuwadziwa ndi ena omwe sitikuwadziwa. Kukacha zonsezi zimabisala 
koma kukada zimatuluka. 

4 "Wanjiru" kapena "Wansanje" uyu ndi munthu amene amanyansidwa 
akamuona mnzake atadalitsidwa ndi dalitso la mtundu uliwonse. Ndipo 
amakhumba kuti dalitsolo limuchokere ngakhale kuti lisamufikire iye. Njiru ndi 
tchimo lalikulu ndiponso ndi nthenda yoipa kwambiri. Mwina munthu wanjiru 
amabisa njiru yake mumtima mpaka kufa nayo. Apo amapuma iye pamodzi 
ndi anthu aja amene ankawachitira dumbo. Mwina amalephera kuibisa 
mumtima ndipo amaionetsera poyera kotero kuti amachita zotheka kuti 
amuchotsere mnzake uja dalitso lomwe wapatsidwa ndi Mulungu. Akalephera 
izi, amangoganiza za kumupha; njiru iyi ndi yoipa kwambiri. 



Surat 114. An-Nas Juzu 30 



1407 



•>■ 



S \ t ^Ui ij^ 




SURAT AN-NAS CXIV 



" lip 



M'surayi Mulungu wapamwambamwamba akulamula 
Mneneri Wake (SAW) kuti apemphe chitetezo kwa lye kuti 
amteteze kwa woipa wamkulu amene ali wobisika, kotero kuti 
anthu ambiri sakumdziwa chifukwa chakuti amawadzera 
kupyolera kumbali yazilakolako zawo ndi zofiina zawo 
ndikuwagwetsa mzoletsedwa za Mbuye wawo Mulungu. 

Woipa ameneyu ndiye mnong'onezi wazoipa yemwe 
amalephera kugwira ntchito yake ngati munthu uja atapempha 
chitetezo kwa Mulungu. Zonong'oneza zake zimakhala za 
udyerekezi ndi zachinyengo. 



Surat An-Nas CXIV 



W:tmm£\ ?K 



M'dzina la Mulungu, Wachifundo 
Chambiri, Wachisoni 

1. Nena: Ndikudzitchinjiriza ndi 
Mbuye (Mleri) wa anthu (yemwe 
akulinganiza Zinthu zawo). 1 

2. Mfumu ya anthu ( Imene iri 
ndi Mphamvu yochita chirichonse 
pa iwo). 

3. Wopembedzedwa wa anthu. 

4. Kuzoipa za mnong'onezi 
(yemwe Amathira unong'onezi wake 



qWH^* 



— Cwb 






kj&Ku&i&fr 



Mulungu pokhala Mlengi wa anthu ndi amenenso amawalera kuyambira 
pamene ali m'mimba mpaka kumapeto a moyo wawo pano padziko. 
Kuwaleraku kuli muuzimu mthupi mu mpweya, ndi pachilichonse chofunika 
pamoyo wawo. Kuonjezera pa zimenezi adawapatsa nzeru ndi kuwasonyeza 
njira zabwino za dziko lapansi ndi tsiku lomaliza. Ndipo adawalamula 
kuzitsata njirazo. Adawasonyezanso njira zoipa za dziko lino lapansi ndi tsiku 
lomaliza. Ndipo adawalamula kuti azipewe njira zoipazo. 



Surat 114. An-Nas Juzu 30 1408 ? * *>■» 



\ \ i ^Ul djj- 



mmitima Ya anthu) yemwenso 
amabisala (posiya Unong'onezi 
wake ngati mwini mtimawo 
Atankumbukira Mulungu). 1 

5. Yemwe amanong'oneza 
mzifuwa za Anthu. 

6. Wochokera m'ziwanda ndi 
mwa anthu. 






1 Mnong'onezi wazoipa amene amabisala ndiye Satana, yemwe ntchito yake 
ndi kunong'oneza zoipa m'mitima ya anthu pofuna kuwasokeretsa ndi 
kuwaiwalitsa Mulungu. Koma akakumana ndi munthu wa chikhulupiriro cha 
mphamvu kapena yemwe amatamanda kwambiri Mbuye wake Mulungu, 
Satanayo amalephera ndipo amathawa; kubwerera m'mbuyo. 

2 Mchilankhulo cha Chiarabu aliyense woipitsitsa amatchedwa "SHETANI" 
Satana, munthu kapena chiwanda. Satana wa muwanthu ndiwoipitsitsa 
kwambiri kwa anthu kuposa wa m'ziwanda. 



Appendix I 



1409 



ZAMKATIMU 


- MASURAH NDI MA AYAH 


Sflrah 


No. 


Page 


Makki/ 
Madani 


LjLufl 


A^iuall 


^J 


Sjj-JI 


Al-Fatihah 


1 


1 


Makki 


*S> 


> 


> 


ajiuJi 


Al-Baqarah 


2 


2 


Madani 


4JXi 


t 


t 


O^dJl 


Al-'Imran 


3 


103 


Madani 


iJXi 


> %r 


r 


01^ JT 


An-Nisa' 


4 


161 


Madani 


4Jjm 


>i> 


i 


(.l-Ji 


Al-Ma'idah 


5 


225 


Madani 


4JJm 


tto 





OJLJlit 


Al-An'am 


6 


266 


Makki 


i& 


til 


1 


f Ui* 


Al-A'raf 


7 


312 


Makki 


& 


r>t 


V 


<Jt J P , iH 


Al-Anfal 


8 


362 


Madani 


ijx. 


rit 


A 


JUi^l 


At-Taubah 


9 


387 


Madani 


LiXi 


TAV 


\ 


^jji 


Yunus 


10 


427 


Makki 


i£> 


ttv 


> * 


U^Ji 


Hud 


11 


455 


Makki 


& 


too 


>> 


.^ 


Yusuf 


12 


484 


Makki 


iJJ 


£A£ 


>t 


«-i-»ji 


Ar-Ra'd 


13 


512 


Madani 


4JJU 


o>T 


>r 


JLPJJI 


Ibrahim 


14 


527 


Makki 


i£> 


OTV 


W 


p»W 


Al-Hijr 


15 


539 


Makki 


i£> 


or* 


>o 


^» 


An-Nahl 


16 


553 


Makki 


aSj> 


oor 


u 


J-J^ 


Al-Isra' 


17 


583 


Makki 


iS* 


OAT 


w 


*V?» 


Al-Kahf 


18 


609 


Makki 


i£> 


1»* 


>A 


U4&» 


Maryam 


19 


637 


Makki 


i£> 


irv 


>\ 


^ 


Ta-Ha 


20 


655 


Makki 


iJJ 


loo 


t . 


^ 


Al-Anbiya' 


21 


681 


Makki 


&> 


1A^ 


t> 


frUi'it 


Al-Hajj 


22 


701 


Madani 


4Jjm 


V»> 


tt 


^' 


Al-Mu'minun 


23 


721 


Makki 


& 


Vt> 


tr 


0_pjli 


An-Nur 


24 


738 


Madani 


3jjl» 


vrA 


t£ 


J^ 1 


Al-Furqan 


.25 


757 


Makki 


iS* 


Vov 


to 


jliyji 


Ash-Shu' ara' 


26 


773 


Makki 


i£> 


vvr 


ti 


fr»y»lji 


An-Naml 


27 


798 


Makki 


i£> 


V^A 


tv 


J^ 1 


Al-Qasas 


28 


816 


Makki 


& 


AM 


tA 


^^mH 


Al-'Ankabut 


29 


837 


Makki 


aJJ 


Arv 


t* 


O^XjJ* 


Ar-Rum 


30 


853 


Makki 


<£* 


Aor 


r. 


f^' 


Luqman 


31 


868 


Makki 


i£* 


A1A 


r> 


JUiJ 


As-Sajdah 


32 


877 


Makki 


^ 


AW 


rt 


OJL^Jt 


Al-Ahzab 


33 


884 


Madani 


ijx. 


AA£ 


rr 


V»j^l 


Saba' 


34 


908 


Makki 


i£> 


*.A 


rt 


L- 


Fatir 


35 


923 


Makki 


iJJ 


\yr 


To 


>i» 


Ya-Stn 


36 


936 


Makki 


iJJ 


*ri 


ri 


J^- 


As-Saffat 


37 


951 


Makki 


iJJ 


*o> 


rv 


oiiUflit 


Sad 


38 


971 


Makki 


iJJ 


*v> 


rA 


J" 


Az-Zumar 


39 


985 


Makki 


<S* 


*Ao 


r* 


^ 


Ghafir 


40 


1004 


Makki 


*JL> 


> . .£ 


£• 


>^ 


Fussilat 


41 


1023 


Makki 


*JJ 


> .tr 


£> 


cJLas 


Ash-Shura 


42 


1038 


Makki 


iJJ 


> »TA 


it 


i^j^LH 


Az-Zukhruf 


43 


1053 


Makki 


^ 


> .or 


tr 


^j»' 


Ad-Dukhan 


44 


1068 


Makki 


*JJ 


^ »1A 


tt 


01>-jO( 


Al-Jathiyah 


45 


1075 


Makki 


*JL> 


^ »Vo 


to 


AJVJnI 


Al-Ahqaf 


46 


1083 


Makki 


&> 


^ .Ar 


£1 


Jii?-^ 


Muhammad 


47 


1093 


Madani 


ijx» 


^ >*r 


£V 


JUrf 


Al-Fath 


48 


1103 


Madani 


Ljx* 


n .r 


£A 


£*Jt 


Al-Hujurat 


49 


1113 


Madani 


4JJU 


>ur 


£* 


Oly^* 


Qfif 


50 


1119 


Makki 


i£* 


>>m 


o » 


J 


Adh-Dhariyat 


51 


1126 


Makki 


& 


>>ti 


o> 


ObjlJJ* 


At-Tur 


52 


1134 


Makki 


iJJ 


urt 


OT 


jjy» 


An-Najm 


53 


1141 


Makki 


i£> 


> W> 


or 


^J* 


Al-Qamar 


54 


1149 


Makki 


iJJ 


\\i\ 


0£ 


^\ 


Ar-Rahman 


55 


1157 


Madani 


ijxi 


> >oV 


00 


c>^* 


Al-Waqi'ah 


56 


1167 


Makki 


& 


U1V 


01 


4*9(_jJl 


Al-Hadid 


57 


1177 


Madani 


~A->Xa 


> WV 


ov 


JbJJ-l 


Al-Mujadilah 


58 


1187 


Madani 


IJXa 


MAV 


oA 


*hi£i 



Appendix I 



1410 



ZAMKATIMU - MASURAH NDI MA AYAH 


Surah 


No. 


Page 


Makki/ 
Madani 


<jLJI 


^iuoil 


^J 


Sj>-JI 


Al-Hashr 


59 


1196 


Madani 


LjJLt 


s\\\ 


M 


r^ 1 


Al-Mumtahnah 


60 


1204 


Madani 


JUJLt 


> Y • 1 


V 


i^Ui 


As-Saff 


61 


1211 


Madani 


LjJLt 


>Y>> 


*\> 


ui*aJl 


Al-Jumu'ah 


62 


1216 


Madani 


4JJL* 


>YU 


*\t 


4*Jri 


Al-Munafiqun 


63 


1221 


Madani 


4JJL* 


>YY> 


nr 


JtASUlt 


At-Taghabun 


64 


1226 


Madani 


4JJLI 


>YY*\ 


*\i 


**»» 


At-Talaq 


65 


1232 


Madani 


4JX* 


>Yrt 


no 


J*W» 


At-Tahrim 


66 


1237 


Madani 


4JJL* 


>Yrv 


*n 


<V«li 


Al-Mulk 


67 


1243 


Makki 


££, 


>Yir 


•\v 


r ddii 


Al-Qalam 


68 


1250 


Makki 


ii. 


>Y©. 


*\A 


^, 


Al-Haqqah 


69 


1258 


Makki 


aSj> 


>Y0A 


H 


AiU-\ 


Al-Ma'arij 


70 


1265 


Makki 


4X. 


>Y*\o 


v. 


CJ^ 


Nun 


71 


1271 


Makki 


i&> 


>YV> 


V> 


C-^ 


Al-Jinn 


72 


1277 


Makki 


i£. 


>YVV 


VY 


& 


AL-Muzzammil 


73 


1283 


Makki 


££, 


>YAr 


vr 


J*>1 


AL-Muddaththir 


74 


1288 


Makki 


;l£. 


>YAA 


VI 


y^ 


Al-Qiyamah 


75 


1295 


Makki 


<£• 


>Y*o 


Vo 


JUiLill 


Al-Insan 


76 


1300 


Madani 


4JXt 


>r. . 


VI 


JUi^i 


Al-Mursalat 


77 


1306 


Makki 


i£. 


>TM 


vv 


o^L-jli 


An-Naba' 


78 


1312 


Makki 


{£> 


>ymy 


VA 


uJi 


An-Nazi'at 


79 


1317 


Makki 


i&> 


>rw 


v^ 


OlPjLJ\ 


'Abasa 


80 


1323 


Makki 


i&> 


>rYr 


A* 


j-^ 


At-Takwtr 


81 


1328 


Makki 


ii. 


>tya 


A> 


y-j^J' 


Al-Infitar 


82 


1332 


Makki 


ii. 


>YTY 


AY 


jllaiiVl 


Al-Mutaffifii. 


83 


1335 


Makki 


{&> 


>rro 


AT 


j^ikii 


Al-Inshiqaq 


84 


1340 


Makki 


k&> 


>ri. 


Al 


JliiJ^i 


Al-Buruj 


85 


1344 


Makki 


*Sj> 


>rn 


Ao 


c^' 


At-Tariq 


86 


1348 


Makki 


ik. 


>riA 


A*\ 


jjlW\ 


Al-A'la 


87 


1350 


Makki 


ii. 


>ro. 


AV 


J*'v 


Al-Ghashiyah 


88 


1354 


Makki 


C&. 


>rot 


AA 


A-iUJt 


Al-Fajr 


89 


1358 


Makki 


ii. 


>roA 


A* 


>» 


Al-Balad 


90 


1363 


Makki 


ii. 


>Y"\r 


*. 


jJLii 


Ash-Shams 


91 


1366 


Makki 


i&> 


>Y"n 


\\ 


jvtt *'' 


Al-Lail 


92 


1368 


Makki 


;l£. 


>Y"\A 


*Y 


JJ" 


Ad-Duha 


93 


1371 


Makki 


;l£. 


>rv> 


*r 


,,^3' 


Ash-Sharh 


94 


1373 


Makki 


4X. 


> r vr 


^i 


C ^J; 


At-Tin 


95 


1375 


Makki 


4X. 


>rvo 


^o 


obJ« 


AI-'Alaq 


96 


1376 


Makki 


4X. 


>rvn 


^ 


jUi 


Al-Qadr 


97 


1379 


Makki 


i&> 


>rv^ 


*v 


)JJ&\ 


Al-Baiyinah 


98 


1381 


Madani 


AJXt 


>TA> 


*A 


A-..\\ 


Az-Zalzalah 


99 


1383 


Madani 


4JJL* 


>TAT 


^ 


w 


Al-'Adiyat 


100 


1385 


Makki 


ix. 


>rAo 


> . . 


ObiUll 


Al-Qari'ah 


101 


1387 


Makki 


4X. 


>rAV 


> o 


APjlflJl 


At-Takathur 


102 


1389 


Makki 


i£. 


>TA\ 


> .Y 


^. 


Al-'Asr 


103 


1390 


Makki 


i£. 


>r*. 


> »r 


j— J* 


Al-Humazah 


104 


1391 


Makki 


ii. 


>r*> 


> .1 


3^*i* 


AI-FI1 


105 


1393 


Makki 


ii. 


>r^r 


> .0 


J^J^ 


Quraish 


106 


1395 


Makki 


i£. 


>r^© 


> .n 


cr^y 


Al-Ma'Gn 


107 


1397 


Makki 


4X. 


>r^v 


> .V 


j^di 


Al-Kauthar 


108 


1399 


Makki 


i£. 


>r^ 


> .A 


j»jfi» 


Al-Kafirun 


109 


1400 


Makki 


^ 


u. • 


>»^ 


jjyi^H 


An-Nasr 


110 


1402 


Madani 


4JJL* 


>£.Y 


>> . 


^^ 


Al-Masad 


111 


1403 


Makki 


i£j> 


M.r 


>>> 


jlU\ 


Al-Ikhlas 


112 


1405 


Makki 


i£. 


U.o 


>>Y 


^^U^^ 


Al-Falaq 


113 


1406 


Makki 


££, 


U."\ 


>>r 


J^» 


An-Nas 


114 


1407 


Makki 


££, 


M.V 


>u 


^ 






Unduna wa zachisilamu,chuma choperekedwa mnjira ya 
Mulungu, Dawah ndi kutsogolera ku njira yoongoka m'dziko 
la chifumu la Saudi Arabia womwe umayang'anira nyumba 
ya Mfumu Fahd yosindikizira Qur'an yopatulika mumzinda wa 
Madinah Munawwarah, ndiwokondwa kwambiri posindikiza 
buku ili la Qur'an lopatulika lotanthauzidwa m'chichewa. 
Ukupempha Allah kuti alichite kukhala lothandiza kwa 
Asilamu onse, NDI KUTI AMUPATSE MUYANG'ANIRI 
WA Mizikiti iwiri yopatulika mfumu Fahd bin Abdu al-Aziz 
Al-Saud mphoto yoyamba pa khama lake lalikulu pofalitsa 
Buku Lopatulika la Allah. Ndipo Allah ndi mwini kupambana. 




;*/ 



Ufulu wosindikiza ndi Otetezedwa 

ndi Nyumba Ya Mfumu 

Fahd Yosindikizira Qur'an Yolemekezeka 

p.o box 6262-AI Madina Al Munawara 



IT 



j-ILJI *Ujt i^ji^l JL$i jiJJLil i^L* <**j4± 

■m. -Atv- tr-A : dJLo, 

Yr/.A^. YY>,i <£*a 

Yr/.AV : fcU^l^j 
^<\"\. -AiV- tr-A : dLoj 





<m. - AiV- tr- A : «JjLo 3 



(^)(o)(TA-^...)